- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
TITO
Kalata ya Paulo Yolembera Tito
Tito
Tit
KALATA YA PAULO YOLEMBERA
TITO
Ndine Paulo, mtumiki wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Ndinatumidwa kuti nditsogolere amene Mulungu anawasankha ku chikhulupiriro ndi ku chidziwitso cha choonadi chimene chimawafikitsa ku moyo wolemekeza Mulungu ndi kuwapatsa chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu amene sanama, analonjeza nthawi isanayambe. Pa nthawi yake Mulungu, Mpulumutsi wathu anawulula poyera mawu ake ndipo analamula kuti ndipatsidwe udindo wolalikira uthengawu.
Kwa Tito, mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro cha ife tonse:
Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu.
Ntchito ya Tito ku Krete
Ndinakusiya ku Krete kuti ulongosole zonse zimene ndinazisiya zisanathe ndiponso usankhe akulu ampingo mʼmizinda yonse, monga momwe ndinakulamulira. Mkulu wampingo akhale munthu wopanda cholakwa, akhale wa mkazi mmodzi yekha, munthu amene ana ake ndi okhulupirira, osati amakhalidwe oyipa ndi osamvera. Popeza mkulu wa mpingo amayendetsa ntchito za banja la Mulungu, ayenera kukhala wopanda cholakwa, asakhale womva zayekha, kapena wopsa mtima msanga, kapena womwa zoledzeretsa, kapena wandewu, kapena wopeza phindu mwachinyengo. Koma akhale wosamala bwino alendo, wokonda zabwino, wodziretsa, wolungama, woyera mtima ndi wosunga mwambo. Iye ayenera kugwiritsa mawu okhulupirika monga tinaphunzitsira, kuti athe kulimbikitsa ena ndi chiphunzitso choona ndiponso kugonjetsa amene atsutsana nacho.
Kudzudzula Olephera Kuchita Bwino
Paja pali anthu ambiri osaweruzika, makamaka mʼgulu la anthu a mdulidwe, oyankhula nkhani zopanda pake ndi kusocheretsa anzawo. Ayenera kuletsedwa kuyankhula chifukwa akusokoneza mabanja athunthu pophunzitsa zinthu zomwe sayenera kuwaphunzitsa. Iwo amachita izi kuti apeze ndalama mwachinyengo. Mneneri wina, mmodzi wa iwo omwewo anati, “Akrete nthawi zonse ndi amabodza, akhalidwe loyipitsitsa ndiponso alesi adyera.” Mawu amenewa ndi woona. Nʼchifukwa chake, uwadzudzule mwamphamvu, kuti akhale ndi chikhulupiriro choona, kuti asasamalenso nthano za Chiyuda, ndi malamulo a anthu amene akukana choonadi. Kwa oyera mtima, zinthu zonse ndi zoyera, koma kwa amene ndi odetsedwa ndi osakhulupirira, palibe kanthu koyera. Kunena zoona, mitima yawo ndi chikumbumtima chawo, zonse nʼzodetsedwa. Iwo amati amadziwa Mulungu, pamene ndi zochita zawo amamukana. Ndi anthu onyansa ndi osamvera, ndi osayenera kuchita kalikonse kabwino.
Malangizo Osiyanasiyana
Koma iwe uziphunzitsa zogwirizana ndi chiphunzitso choona. Phunzitsa amuna achikulire kuti akhale osaledzera, aulemu wawo, odziletsa, okhwima mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkupirira.
Chimodzimodzinso, phunzitsa amayi achikulire kuti akhale aulemu mʼmakhalidwe awo, asakhale osinjirira anzawo kapena zidakwa, koma akhale alangizi abwino. Tsono atha kulangiza amayi achichepere kukonda amuna awo ndi ana awo. Kuwaphunzitsa kukhala odziletsa ndi oyera mtima, osamala bwino mabanja awo, okoma mtima, ndi ogonjera amuna awo. Choncho palibe amene adzanyoze mawu a Mulungu.
Momwemonso, uwalimbikitse amuna achichepere kuti akhale odziletsa. Pa zonse iwe mwini ukhale chitsanzo pa ntchito zabwino. Pa chiphunzitso chako uwonetsa kuona mtima ndi kutsimikiza mtima kwako. Phunzitsa choonadi kuti anthu asapeze chokutsutsa, motero wotsutsana nawe adzachita manyazi chifukwa adzasowa kanthu koyipa kuti atinenere.
Phunzitsa akapolo kuti azigonjera ambuye awo mu zinthu zonse ndi kuwakondweretsa. Asamatsutsane nawo kapena kumawabera, koma adzionetse kuti ndi odalirika, motero pa zochita zawo zonse adzaonetsa ubwino wa chiphunzitso cha Mulungu, Mpulumutsi wathu.
Pakuti chisomo cha Mulungu chimene chimapulumutsa chaonekera kwa anthu onse. Chisomo chimatiphunzitsa kukana moyo osalemekeza Mulungu komanso zilakolako za dziko lapansi. Ndipo chimatiphunzitsa kukhala moyo odziletsa, olungama ndi opembedza Mulungu nthawi ino, pamene tikudikira chiyembekezo chodala; kuonekera kwa ulemerero wa Mulungu wathu wamkulu ndi Mpulumutsi, Yesu Khristu, amene anadzipereka yekha chifukwa cha ife kutiwombola ku zoyipa zonse ndi kudziyeretsera yekha anthu amene ndi akeake, achangu pa ntchito yabwino.
Tsono zimenezi ndi zinthu zomwe uyenera kuphunzitsa. Uziwalimbikitsa anthu ndi kuwatsutsa komwe. Uzichita zimenezi ndi ulamuliro wonse. Wina aliyense asakupeputse ayi.
Kuchita Ntchito Zabwino
Uwakumbutse anthu kuti azigonjera oweruza ndi olamulira, aziwamvera ndi kukhala okonzeka kuchita chilichonse chabwino. Asamachitire chipongwe aliyense, asamakangane, akhale ofatsa ndipo oganizira ena, ndipo nthawi zonse akhale aulemu kwa anthu onse.
Nthawi ina tinali opusa, osamvera, onamizidwa ndi omangidwa ndi zilakolako ndi zokondweretsa zamitundumitundu. Tinkakhala moyo wadumbo ndi wakaduka, odedwa ndiponso odana wina ndi mnzake. Koma kukoma mtima ndi chikondi cha Mulungu Mpulumutsi wathu chitaonekera, Iye anatipulumutsa, osati chifukwa cha ntchito zathu zolungama zimene tinachita koma chifukwa cha chifundo chake. Anatipulumutsa potisambitsa, kutibadwitsa kwatsopano ndi kutikonzanso mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa mowolowamanja kudzera mwa Yesu Khristu Mpulumutsi wathu, kuti titalungamitsidwa mwachisomo chake, tikhale olowamʼmalo okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha. Mawuwa ndi okhulupirika ndipo ine ndikufuna kuti iwe utsindike zinthu izi, kuti amene akhulupirira Mulungu adzipereke kuchita ntchito zabwino. Zinthu izi ndi zabwino kwambiri ndi zopindulitsa kwa aliyense.
Koma upewe kufufuzafufuza zopusa, kuwerengawerenga mndandanda wa mibado ya makolo, mikangano ndi mitsutso pa za Malamulo, chifukwa zimenezi ndi zosapindulitsa ndi zopanda pake. Munthu woyambitsa mipatuko umuchenjeze koyamba, ndiponso umuchenjeze kachiwiri. Kenaka umupewe. Iwe udziwe kuti munthu wotero ngosokoneza ndi wochimwa, ndipo akudzitsutsa yekha.
Mawu Otsiriza
Ndikadzamutuma Artema kapena Tukiko kwanuko, udzayesetse kundipeza ku Nikapoli, chifukwa ndatsimikiza kukhala kumeneko pa nthawi yozizira. Uyesetse chilichonse ungathe kuthandiza Zena katswiri wa malamulo ndi Apolo, kuti apitirize ulendo wawo, ndipo uwonetsetse asasowe kanthu. Anthu athu aphunzire kudzipereka pogwira ntchito zabwino, nʼcholinga chakuti athandize zinthu zimene zikufunika msangamsanga. Ndipo asakhale moyo osapindulitsa.
Onse amene ali ndi ine akupereka moni. Upereke moni kwa amene amatikonda ife mʼchikhulupiriro.
Chisomo chikhale ndi inu nonse.