- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
NAHUMU
Nahumu
Nahumu
Nah
Nahumu
Uthenga wonena za Ninive. Buku la masomphenya a Nahumu wa ku Elikosi.
Mkwiyo wa Yehova pa Ninive
Yehova ndi Mulungu wansanje
ndiponso wobwezera;
Yehova amabwezera ndipo ndi waukali.
Yehova amabwezera adani ake
ndipo ukali wake umakhala nthawi zonse pa adani akewo.
Yehova sakwiya msanga koma ndi wa mphamvu yayikulu;
ndipo sadzalola kuti munthu
wolakwa asalangidwe.
Iye amayenda mʼkamvuluvulu ndi mʼnamondwe,
ndipo mitambo ndi fumbi la ku mapazi ake.
Amalamulira nyanja ndipo imawuma;
amawumitsa mitsinje yonse.
Zomera za ku Basani ndi Karimeli zimawuma
ndipo maluwa a ku Lebanoni amafota.
Mapiri amagwedera pamaso pake
ndipo zitunda zimasungunuka.
Dziko lapansi limanjenjemera pamaso pake,
dziko lonse ndi zonse zokhala mʼmenemo.
Ndani angathe kuyima pamaso pake Iye akalusa?
Ndani angapirire mkwiyo wake woopsa?
Ukali wake ukuyaka ngati moto;
matanthwe akunyeka pamaso pake.
Yehova ndi wabwino,
ndiye kothawirako nthawi ya masautso.
Amasamalira amene amamudalira,
koma ndi madzi achigumula choopsa
Iye adzawononga adani ake (Ninive);
adzapirikitsira adani ake ku malo a mdima.
Chiwembu chilichonse chimene akukonzekera kumuchitira Yehova
adzachiwononga kotheratu;
msautso sudzabweranso kachiwiri.
Iwo adzakodwa mu ziyangoyango za minga
ndipo adzaledzera ndi vinyo wawo;
adzatenthedwa ngati ziputu zowuma.
Kwa iwe, Ninive, kunachokera munthu wa cholinga choyipa,
wofuna kuchitira Yehova chiwembu,
amene amapereka uphungu woyipa.
Yehova akuti,
“Ngakhale Asiriyawo ali ndi abwenzi,
kaya iwowo ndi ambiri,
koma adzawonongedwa ndi kutheratu.
Ngakhale ndinakuzunza iwe Yuda,
sindidzakuzunzanso.
Tsopano ndidzathyola goli lake pa khosi lako
ndipo ndidzadula maunyolo ako.”
Yehova walamulira za iwe, Ninive kuti,
“Sudzakhala ndi zidzukulu
zimene zidzadziwike ndi dzina lako.
Ndidzawononga zifanizo zosema ndi mafano owumba
amene ali mʼnyumba ya milungu yako.
Ine ndidzakukumbira manda
chifukwa ndiwe woyipitsitsa.”
Taonani, pa phiripo,
mapazi a munthu amene akubweretsa nkhani yabwino,
amene akulengeza za mtendere!
Inu anthu a ku Yuda, chitani madyerero anu
ndipo kwaniritsani malumbiro anu.
Anthu oyipa sadzakuthiraninso nkhondo;
iwo adzawonongedwa kotheratu.
Kugwa kwa Ninive
Wodzathira nkhondo akubwera
kudzalimbana nawe, Ninive.
Tetezani malinga anu,
dziyangʼanani ku msewu,
konzekerani nkhondo,
valani dzilimbe.
Yehova adzabwezeretsa ulemerero wa Yakobo
ngati ulemerero wa Israeli,
ngakhale anthu owononga anawawononga kotheratu
ndipo anawononganso mpesa wawo.
Zishango za ankhondo ake ndi zofiira;
asilikali ake avala zovala zofiirira.
Zitsulo za pa magaleta zikunyezimira
tsiku la kukonzekera kwake.
Akuonetsa mikondo ya mkungudza yonoledwa.
Magaleta akuthamanga mʼmisewu
akungothamangathamanga pa mabwalo.
Akuoneka ngati miyuni yoyaka;
akuthamanga ngati chingʼaningʼani.
Iye akuyitanitsa asilikali ake wolemekezeka,
koma iwo akubwera napunthwa.
Akuthamangira ku linga la mzinda;
akuyimika chodzitchinjirizira pamalo pake.
Atsekula zipata zotchinga madzi a mu mtsinje
ndipo nyumba yaufumu yagwa.
Zatsimikizika kuti mzinda
utengedwa ndi kupita ku ukapolo.
Akapolo aakazi akulira ngati nkhunda
ndipo akudziguguda pachifuwa.
Ninive ali ngati dziwe,
ndipo madzi ake akutayika.
Iwo akufuwula kuti, “Imani! Imani!”
Koma palibe amene akubwerera.
Funkhani siliva!
Funkhani golide!
Katundu wake ndi wochuluka kwambiri,
chuma chochokera pa zinthu zake zamtengowapatali!
Iye wawonongedwa, wafunkhidwa ndipo wavulidwa!
Mitima yasweka, mawondo akuwombana,
anthu akunjenjemera ndipo
nkhope zasandulika ndi mantha.
Kodi tsopano dzenje la mikango lili kuti,
malo amene mikango inkadyetserako ana ake,
kumene mkango waumuna ndi waukazi unkapitako,
ndipo ana a mkango sankaopa kanthu kalikonse?
Mkango waumuna unkapha nyama yokwanira ana ake
ndiponso kuphera nyama mkango waukazi,
kudzaza phanga lake ndi zimene wapha
ndiponso dzenje lake ndi nyama imene waphayo.
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndikutsutsana nawe.
Ndidzatentha magaleta ako mpaka utsi tolotolo,
ndipo lupanga lidzapha mikango yako yayingʼono;
sindidzakusiyira chilichonse choti udye pa dziko lapansi.
Mawu a amithenga anu sadzamvekanso.”
Tsoka la Ninive
Tsoka kwa mzinda wopha anthu,
mzinda wodzaza ndi mabodza,
mzinda wodzaza ndi anthu olanda zinthu anzawo,
mu mzinda mʼmene simusowa anthu osautsidwa nthawi zonse!
Kulira kwa zikwapu,
mkokomo wa mikombero,
kufuwula kwa akavalo
ndiponso phokoso la magaleta!
Kuthamanga kwa anthu okwera pa akavalo,
kungʼanima kwa malupanga
ndi kunyezimira kwa mikondo!
Anthu ambiri ophedwa,
milumilu ya anthu akufa,
mitembo yosawerengeka,
anthu akupunthwa pa mitemboyo.
Zonsezi ndi chifukwa cha zilakolako za mkazi wachiwerewere,
wokopa anthu uja, mkazi wochita zamatsenga,
amene anakopa mitundu ya anthu ndi zachiwerewere zake,
ndiponso anthu a mitundu ina ndi zaufiti zake.
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndikutsutsana nawe.
Ndidzakuvula chovala chako.
Anthu a mitundu ina ndidzawaonetsa umaliseche wako
ndipo udzachita manyazi pamaso pa maufumu onse.
Ndidzakuthira zonyansa,
ndidzakuchititsa manyazi
ndiponso kukusandutsa chinthu choseketsa.
Onse amene adzakuona adzakuthawa ndipo adzati,
‘Ninive wasanduka bwinja,
adzamulira ndani?’
Kodi ndingamupeze kuti munthu woti nʼkukutonthoza?”
Kodi ndiwe wopambana Tebesi,
mzinda wokhala mʼmbali mwa Nailo,
wozunguliridwa ndi madzi?
Mtsinjewo unali chitetezo chake,
madziwo anali linga lake.
Mphamvu zake zinali Kusi ndi Igupto,
Puti ndi Libiya anali ena mwa abwenzi ake.
Komabe anthu a ku Tebesi anagwidwa
ndipo anapita ku ukapolo.
Ana ake anawaphwanyitsa pansi
mʼmisewu yonse ya mu mzindamo.
Anachita maere ogawana anthu ake otchuka,
ndipo anthu ake onse amphamvu
anamangidwa ndi maunyolo.
Iwenso Ninive udzaledzera;
udzabisala
ndipo udzafunafuna malo othawirako kuopa mdani.
Malo ako onse otetezedwa ali ngati mitengo ya mkuyu
yokhala ndi zipatso zoyambirira kucha;
pamene agwedeza mitengoyo,
nkhuyuzo zimagwera mʼkamwa mwa wofuna kuzidya.
Tayangʼana ankhondo ako,
onse ali ngati akazi!
Zipata za dziko lako zatsekukira adani ako;
moto wapsereza mipiringidzo yake.
Tungani madzi woti mudzamwe nthawi ya kuzunguliridwa kwanu,
limbitsani chitetezo chanu!
Pondani dothi,
ikani mʼchikombole,
konzani khoma la njerwa!
Kumeneko moto udzakupserezani;
lupanga lidzakukanthani
ndipo lidzakuwonongani ngati likuwononga ziwala.
Chulukanani ngati ziwala,
chulukanani ngati dzombe!
Mwachulukitsa chiwerengero cha anthu a malonda anu
mpaka kupambana nyenyezi za mlengalenga,
koma iwo ngati dzombe akuwononga dziko
ndipo kenaka akuwuluka nʼkuchoka.
Akalonga ako ali ngati dzombe,
akuluakulu ako ali ngati gulu la dzombe
limene lamatirira pa khoma nthawi yozizira,
koma pamene dzuwa latuluka limawuluka,
ndipo palibe amene amadziwa komwe lapita.
Iwe mfumu ya ku Asiriya,
abusa ako agona tulo;
anthu ako olemekezeka amwalira.
Anthu ako amwazikira ku mapiri
popanda ndi mmodzi yemwe wowasonkhanitsa.
Palibe chimene chingachize bala lako;
chilonda chako sichingapole.
Aliyense amene amamva za iwe
amawomba mʼmanja chifukwa cha kugwa kwako,
kodi alipo amene sanazilawepo
nkhanza zako zosatha?