- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
MARKO
Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Marko
Marko
Mk
UTHENGA WABWINO WA YESU KHRISTU WOLEMBEDWA NDI
MARKO
Yohane Mʼbatizi Akonza Njira
Chiyambi cha Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu, Mwana wa Mulungu, monga zalembedwera mʼbuku la mneneri Yesaya:
“Ine ndidzatuma mthenga wanga patsogolo panu,
amene adzakonza njira yanu,”
“Mawu a wofuwula mʼchipululu,
‘Konzani njira ya Ambuye,
wongolani njira zake.’ ”
Ndipo Yohane anabwera mʼmadera a mʼchipululu nabatiza, ndi kulalikira za ubatizo wa kutembenuka mtima ndi wa chikhululukiro cha machimo. Madera onse a ku Yudeya ndi anthu onse a ku Yerusalemu anatuluka napita kwa iye. Akavomereza machimo awo, amawabatiza mu mtsinje wa Yorodani. Yohane amavala zovala zopangidwa ndi ubweya wangamira, ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake, ndipo amadya dzombe ndi uchi wamthengo. Ndipo uthenga wake unali uwu: “Pambuyo panga pakubwera wina wondiposa ine mphamvu. Ine si woyenera kuwerama ndi kumasula zingwe za nsapato zake. Ine ndikubatizani ndi madzi, koma Iye adzakubatizani ndi Mzimu Woyera.”
Kubatizidwa ndi Kuyesedwa kwa Yesu
Pa nthawi imeneyo Yesu anabwera kuchokera ku Nazareti wa ku Galileya ndipo anabatizidwa ndi Yohane mu mtsinje wa Yorodani. Pamene Yesu ankatuluka mʼmadzi, anaona kumwamba kukutsekuka ndipo Mzimu Woyera akutsikira pa Iye ngati nkhunda. Ndipo Mawu anamveka kuchokera kumwamba: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa; ndipo ndikondwera nawe.”
Nthawi yomweyo Mzimu Woyera anamutumiza Iye ku chipululu, ndipo anali mʼchipululumo masiku makumi anayi, akuyesedwa ndi Satana. Anali pakati pa nyama zakuthengo; ndipo angelo anamutumikira.
Yesu Alengeza za Uthenga Wabwino
Yohane atamutsekera mʼndende, Yesu anapita ku Galileya nalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu nati, “Nthawi yafika, ufumu wa Mulungu wayandikira. Tembenukani mtima ndi kukhulupirira Uthenga Wabwino!”
Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba
Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Simoni ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja, popeza anali asodzi. Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine, ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.
Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo, ali mʼbwato akukonza makoka awo. Mosataya nthawi anawayitana, ndipo anasiya abambo awo Zebedayo ndi anyamata aganyu ali mʼbwatomo, namutsata Iye.
Yesu Atulutsa Mzimu Woyipa
Iwo anapita ku Kaperenawo, ndipo tsiku la Sabata litafika, Yesu analowa mʼsunagoge nayamba kuphunzitsa. Anthu anadabwa ndi chiphunzitso chake, chifukwa anawaphunzitsa ngati munthu amene anali ndi ulamuliro, osati ngati aphunzitsi amalamulo. Pomwepo munthu wina mʼsunagogemo amene anali wogwidwa ndi mzimu woyipa anafuwula kuti, “Mukufuna chiyani kwa ife, Yesu wa ku Nazareti? Kodi mwabwera kudzatiwononga? Ndikudziwa kuti ndinu ndani, ndinu Woyerayo wa Mulungu!”
Yesu anadzudzula chiwandacho mwamphamvu nati, “Khala chete! Tuluka mwa iye!” Mzimu woyipawo unamugwedeza mwamphamvu ndipo unatuluka mwa iye ukufuwula.
Anthu anadabwa kwambiri kotero kuti anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Ichi nʼchiyani? Chiphunzitso chatsopano ndi ulamuliro! Iye akulamula, ngakhale mizimu yoyipa ikumumvera.” Mbiri yake inafalikira kudera lonse la Galileya mofulumira.
Yesu Achiritsa Anthu Ambiri
Atangochoka mu sunagoge, Yesu pamodzi ndi Yakobo ndi Yohane anakalowa mʼnyumba ya Simoni ndi Andreya. Mpongozi wa Simoni anali chigonere akudwala malungo, ndipo anamuwuza Yesu za iye. Ndipo Yesu anapita kwa iye, namugwira dzanja namuthandiza kudzuka. Malungo anachoka ndipo anayamba kuwatumikira.
Madzulo omwewo dzuwa litalowa anthu anabweretsa kwa Yesu anthu onse odwala ndi ogwidwa ndi ziwanda. Anthu onse a mʼmudzimo anasonkhana pa khomo, Yesu anachiritsa ambiri amene anali ndi matenda osiyanasiyana, komanso anatulutsa ziwanda zambiri, ndipo sanalole kuti ziwandazo ziyankhule chifukwa zinkamudziwa Iye.
Yesu Apemphera Kumalo a Yekha
Mmamawa, kukanali kamdima, Yesu anadzuka, nachoka pa nyumbapo kupita kumalo kwa yekha, kumene anakapemphera. Simoni ndi anzake anapita kokamufunafuna Iye, ndipo atamupeza, anamuwuza kuti, “Aliyense akukufunani!”
Yesu anayakha kuti, “Tiyeni tipite kwina ku midzi ya pafupi kuti ndikalalikirenso kumeneko. Ichi ndi chifukwa chimene ndinabwerera.” Potero anayendayenda mu Galileya, kulalikira mʼmasunagoge awo ndi kutulutsa ziwanda.
Yesu Achiritsa Wakhate
Munthu wakhate anabwera kwa Iye, nagwada, namupempha kuti, “Ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
Yesu pomva naye chifundo, anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo nati, “Ndikufuna, yeretsedwa!” Nthawi yomweyo khate linachoka ndipo anachiritsidwa.
Nthawi yomweyo Yesu anamuwuza kuti apite koma anamuchenjeza kuti, “Wonetsetsa kuti usawuze aliyense za zimenezi. Koma pita, kadzionetse wekha kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose analamulira zotsimikizira kuyeretsedwa kwanu, ngati umboni kwa iwo.” Mʼmalo mwake anapita nayamba kuyankhula momasuka, nafalitsa mbiriyo. Zotsatira zake, Yesu sanathe kulowa mʼmudzi moonekera, koma anakhala kunja kumalo kopanda anthu. Komabe anthu amabwera kwa Iye kuchokera kulikonse.
Yesu Achiritsa Munthu Wofa Ziwalo
Patapita masiku pangʼono, Yesu atalowanso mu Kaperenawo, zinamveka kuti wabwera ali mʼnyumba. Choncho anthu ambiri anasonkhana kotero kuti panalibenso malo, ngakhale ndi pa khomo pomwe, ndipo Iye anawalalikira mawu. Amuna anayi anabwera, atanyamula munthu wofa ziwalo. Popeza sakanatha kufika naye kwa Yesu chifukwa cha gulu la anthu, anasasula denga chapamwamba pamene panali Yesu, ndipo atabowoleza, anatsitsa mphasa yomwe munthu wofa ziwaloyo anagonapo. Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati kwa wofa ziwaloyo, “Mwana, machimo ako akhululukidwa.”
Ndipo ena mwa aphunzitsi amalamulo anakhala pansi pomwepo, namaganiza mʼmitima mwawo kuti, “Nʼchifukwa chiyani munthuyu ayankhula chotere? Iye akuchitira mwano Mulungu! Ndani angakhululukire munthu machimo kupatula Mulungu yekha?”
Nthawi yomweyo Yesu anadziwa mu mzimu wake kuti izi ndi zimene ankaganiza mʼmitima yawo, ndipo anawawuza kuti, “Chifukwa chiyani mukuganiza zinthu izi? Chapafupi nʼchiyani; kunena kwa wofa ziwaloyu kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kuti, ‘Imirira, tenga mphasa yako ndipo yenda?’ Koma kuti mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo.” Anati kwa wofa ziwaloyo, “Ndikuwuza iwe, imirira, tenga mphasa yako ndipo pita kwanu.” Anayimirira, nanyamula mphasa yake natuluka onse akumuona. Izi zinadabwitsa aliyense ndipo anayamika Mulungu nati, “Sitinaonepo zinthu ngati izi!”
Kuyitanidwa kwa Levi
Yesu anatulukanso napita kumbali ya nyanja. Gulu lalikulu la anthu linabwera kwa Iye, ndipo anayamba kuliphunzitsa. Pamene ankayendabe, anaona Levi mwana wa Alufeyo atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anamuwuza kuti, “Tsate Ine.” Ndipo Levi anayimirira namutsata Iye.
Yesu atakalandira chakudya ku nyumba kwa Levi, amisonkho ambiri ndi “ochimwa” ankadya naye pamodzi ndi ophunzira ake, pakuti anali ambiri amene anamutsatira. Pamene aphunzitsi amalamulo a Afarisi anamuona akudya ndi “ochimwa” ndi amisonkho, anafunsa ophunzira ake kuti, “Chifukwa chiyani amadya ndi olandira msonkho ndi ochimwa?”
Yesu atamva zimenezi, anawawuza kuti, “Anthu amene ali bwino safuna singʼanga koma odwala. Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa.”
Za Kusala Kudya
Ndipo ophunzira a Yohane ndi a Afarisi amasala kudya. Anthu ena anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Zitheka bwanji kuti ophunzira a Yohane ndi ophunzira a Afarisi amasala kudya, koma anu satero?”
Yesu anayankha nati, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya bwanji pamene iye ali nawo pamodzi? Iwo sangatero, pamene iye ali nawo pamodzi. Koma nthawi idzafika pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa tsiku limenelo adzasala kudya.
“Palibe amene amasokerera chigamba chatsopano pa chovala chakale. Ngati atatero, chigamba chatsopanocho chidzazomola chovala chakalecho, kukulitsa chibowocho. Ndipo palibe amene amathira vinyo watsopano mʼmatumba akale a vinyo. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa matumba a vinyo ndipo vinyoyo pamodzi ndi matumbawo zidzawonongeka. Ayi, satero, amathira vinyo watsopano mʼmatumba atsopanonso.”
Yesu Mbuye wa Sabata
Tsiku lina la Sabata, Yesu amadutsa pakati pa minda ya tirigu, ndipo ophunzira ake amayenda naye limodzi, nayamba kubudula ngala za tiriguyo. Afarisi anati kwa Iye, “Taonani, chifukwa chiyani akuchita chosaloledwa ndi lamulo pa Sabata?”
Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali osowa ndi anamva njala? Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.”
Pamenepo anawawuza kuti, “Sabata linapangidwira munthu, osati munthu kupangidwira Sabata. Choncho Mwana wa Munthu ali Ambuye ngakhale wa Sabata.”
Yesu Achiritsa Wolumala Dzanja
Nthawi inanso analowa mʼsunagoge, ndipo munthu wa dzanja lolumala anali momwemo. Ena a iwo anafunafuna chifukwa chakuti akamuneneze Yesu, potero anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angamuchiritse tsiku la Sabata. Yesu anati kwa munthu wolumala dzanjayo, “Imirira, bwera kuno kutsogolo.”
Ndipo Yesu anawafunsa kuti, “Kodi chololedwa ndi chiyani pa tsiku la Sabata: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kupha?” Koma iwo anakhala chete.
Yesu anawayangʼana ndi mkwiyo ndipo powawidwa mtima chifukwa cha mitima yawo yowuma anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye analiwongola, ndipo dzanja lake linachira. Kenaka Afarisi anatuluka nayamba kukonza chiwembu ndi Aherode mmene angamuphere Yesu.
Magulu a Anthu Amutsata Yesu
Yesu anachoka pamodzi ndi ophunzira ake napita ku nyanja, ndipo gulu lalikulu la anthu lochokera ku Galileya linamutsata. Atamva zonse zimene amachita, anthu ambiri anabwera kwa Iye kuchokera ku Yudeya, Yerusalemu, Idumeya ndi madera a ku tsidya kwa mtsinje wa Yorodani ndi ozungulira Turo ndi Sidoni. Chifukwa cha gulu la anthu, anawuza ophunzira ake kuti apezeretu bwato likhale, kuti anthu angamupanikize. Pakuti anachiritsa ambiri, kotero kuti iwo amene anali ndi matenda amakankhana kutsogolo kuti amukhudze. Nthawi iliyonse mizimu yoyipa ikamuona, imagwa pansi pamaso pake ndi kufuwula kuti, “Inu ndinu Mwana wa Mulungu!” Koma anayichenjeza mwamphamvu kuti isanene kuti Iye anali ndani.
Yesu Asankha Ophunzira Khumi ndi Awiri
Yesu anakwera ku phiri ndipo anayitana amene anawafuna, ndipo anabwera kwa Iye. Iye anasankha khumi ndi awiri, nawayika akhale atumwi; pokhala ndi Iye aziwatuma kukalalikira ndi kuti akhale ndi ulamuliro wotulutsa ziwanda. Awa ndi khumi ndi awiri amene anawasankha: Simoni (amene anapatsidwa dzina lakuti Petro); Yakobo mwana wa Zebedayo, ndi mʼbale wake Yohane (iwowa anawapatsa dzina lakuti Bowanege, ndiye kuti ana a bingu); Andreya, Filipo, Bartumeyu, Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Tadeyo, Simoni Zelote, ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.
Yesu ndi Belezebabu
Pambuyo pake Yesu analowa mʼnyumba, ndipo gulu la anthu linasonkhananso, kotero kuti Iye pamodzi ndi ophunzira ake sanapeze mpata kuti adye. Anthu a ku banja lake atamva zimenezi, anapita kuti akamutenga, pakuti ankanena kuti, “Wazungulira mutu.”
Ndipo aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anati, “Iye wagwidwa ndi Belezebabu! Ndi ulamuliro wa mkulu wa ziwanda akutulutsa ziwanda.”
Pamenepo Yesu anawayitana nawayankhula mʼmafanizo nati: “Kodi Satana angatulutse bwanji Satana? Ngati ufumu ugawanikana mwa iwo okha, ufumu umenewo sungakhalitse. Ngati nyumba igawanikana mwa iyo yokha, nyumba imeneyo singathe kuyima. Ndipo ngati Satana adzitsutsa yekha sangathe kuyima; ulamuliro wake watha. Kunena zoona, palibe munthu angalowe mʼnyumba ya munthu wamphamvu ndi kutenga katundu wake pokhapokha atayamba wamumanga munthu wamphamvuyo. Pamenepo akhoza kumubera. Ndikukuwuzani zoona kuti machimo onse ndi zamwano zonse za anthu zidzakhululukidwa, koma aliyense amene achitira mwano Mzimu Woyera sadzakhululukidwa pakuti wachita tchimo losatha.”
Ananena izi chifukwa anati, “Ali ndi mzimu woyipa.”
Amayi ndi Abale ake a Yesu
Pamenepo amayi ndi abale ake a Yesu anafika. Atayima kunja, anatuma wina kuti akamuyitane Iye. Gulu la anthu linakhala momuzungulira Iye, ndipo anamuwuza kuti, “Amayi ndi abale anu ali panja akukufunani.”
Iye anafunsa kuti, “Amayi ndi abale anga ndi ndani?”
Pamenepo anayangʼana anthu amene anakhala momuzungurira ndipo anati, “Awa ndi amayi anga ndi abale anga! Aliyense amene achita chifuniro cha Mulungu ndi mʼbale wanga ndi mlongo wanga ndi amayi anga.”
Fanizo la Wofesa Mbewu
Nthawi inanso Yesu atakhala mʼmbali mwa nyanja, anayamba kuphunzitsa. Gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira kotero kuti Iye analowa mʼbwato lomwe linali pa nyanja nakhalamo, anthu onse ali pa mtunda mʼmbali mwa madzi. Anawaphunzitsa zinthu zambiri mʼmafanizo, ndipo mʼchiphunzitso chake anati: “Tamverani! Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. Akufesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa njira, ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. Zina zinagwa pa malo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. Koma dzuwa litakwera, mbewuzo zinapserera, ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. Mbewu zina zinagwa pa minga, ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. Mbewu zinanso zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinamera, zinakula ndi kubereka zipatso, zina zochuluka makumi atatu, zina makumi asanu ndi limodzi ndi zina 100.”
Pamenepo Yesu anati, “Amene ali ndi makutu akumva, amve.”
Ali yekha, ophunzira ndi ena omuzungulira, anamufunsa za mafanizo. Iye anawawuza kuti, “Chinsinsi cha ufumu wa Mulungu chapatsidwa kwa inu. Koma kwa amene ali kunja zinthu zonse zinenedwa mʼmafanizo: kotero kuti,
“ ‘Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu,
kumva mudzamva koma osamvetsetsa,
kuti mwina angatembenuke ndi kukhululukidwa!’ ”
Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Kodi simukulimvetsa fanizoli? Kodi nanga mudzazindikira bwanji fanizo lina lililonse? Wofesa amafesa mawu. Anthu ena ali ngati mbewu za mʼmbali mwa njira, mʼmene mawu amafesedwamo. Akangowamva, Satana amabwera ndi kuchotsa mawu amene anafesedwa mwa iwo. Ena, monga mbewu zofesedwa pa miyala, amamva mawu ndipo nthawi yomweyo amawalandira ndi chimwemwe. Koma popeza alibe mizu, amakhala kwa kanthawi kochepa. Mavuto kapena masautso akafika chifukwa cha mawu, amagwa mofulumira. Komabe ena, monga mbewu zofesedwa pakati pa minga, amamva mawu; koma nkhawa zamoyo uno, chinyengo cha chuma ndi zokhumba za zinthu zina zimabwera ndi kutchinga mawu, ndipo amawachititsa kukhala osabala chipatso. Ena, ngati mbewu zofesedwa pa nthaka yabwino, amamva mawu, nawalandira, ndi kubereka zipatso zokwanira makumi atatu, makumi asanu ndi limodzi, kapena ngakhale 100 kuwonjezera pa zomwe zinafesedwa.”
Fanizo la Nyale
Iye anawawuza kuti, “Kodi umatenga nyale ndi kuyiika pansi pa mbiya kapena pansi pa bedi? Mʼmalo mwake, kodi simuyika pa choyikapo chake? Pakuti chilichonse chobisika chidzayenera kuwululika, ndi chilichonse chachinsinsi chidzayenera kuonekera poyera. Ngati wina ali ndi makutu akumva, amve.”
Anapitiriza nati, “Ganizirani mosamala zimene mukumva, ndi muyeso umene mugwiritsa ntchito, mudzayesedwa nawo, ndipo ngakhale kwambiri. Amene ali nazo adzapatsidwa zochuluka; amene alibe, ngakhale zimene ali nazo zidzachotsedwa kwa iwo.”
Fanizo la Mbewu Imene Ikukula
Iye anatinso, “Umu ndi mmene ulili ufumu wa Mulungu. Munthu amafesa mbewu mʼnthaka. Usiku ndi usana, kaya agona kapena adzuka, mbewu imamera ndi kukula, ngakhale sadziwa mmene zimachitikira. Nthaka pa yokha imatulutsa mbewu, umayamba mʼmera, kenaka ngala, kenaka mbewu yokhwima mʼngalayo. Mbewuyo ikangokhwima, amayimweta chifukwa nthawi yokolola yakwana.”
Fanizo la Mbewu ya Mpiru
Ndipo anatinso, “Kodi tinene kuti ufumu wa Mulungu ufanana ndi chiyani, kapena ndi fanizo lotani limene tidzagwiritsa ntchito pakuwufotokozera? Uli ngati mbewu ya mpiru imene ndi mbewu yayingʼono kwambiri yomwe mumadzala mʼnthaka. Koma ikadzalidwa, imakula ndi kukhala yayikulu koposa mbewu zina zonse za mʼmunda ndipo mʼnthambi zake zazikulu mbalame zamlengalenga zimadzapuma pa mthunzi wake.”
Ndi mafanizo ambiri onga awa Yesu anayankhula mawu kwa iwo, monga mmene akanatha kumvetsa. Iye sananene kanthu kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. Koma ali yekha ndi ophunzira ake, ankawatanthauzira zonse.
Yesu Aletsa Namondwe
Tsiku limenelo atafika madzulo, anawuza ophunzira ake kuti, “Tiyeni tiwolokere tsidya lina.” Atasiya gulu la anthu mʼmbuyo, anamutenga Iye, napita naye monga momwe anali mʼbwatolo. Panalinso mabwato ena pamodzi ndi Iye. Mphepo yamkuntho inabuka, ndipo mafunde anawomba bwatolo, kotero kuti linali pafupi kumira. Pa nthawi imeneyi Yesu anali akugona atatsamira pilo kumbuyo kwa bwato. Ophunzira anamudzutsa nati kwa Iye, “Aphunzitsi, kodi simukusamala kuti timira?”
Yesu anauka nadzudzula mphepo nati kwa mafunde, “Chete! Khala bata!” Pamenepo mphepo inaleka ndipo kunachita bata.
Iye anati kwa ophunzira ake, “Muli ndi mantha chifukwa chiyani? Kodi mukanalibe chikhulupiriro?”
Iwo anachita mantha nafunsana wina ndi mnzake kuti, “Uyu ndani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvera Iye!”
Yesu Achiritsa Wogwidwa ndi Ziwanda
Ndipo anawoloka nyanja napita ku dera la Gerasa. Yesu atatuluka mʼbwato, munthu amene anali ndi mzimu woyipa anachoka ku manda ndi kukumana naye. Munthuyu amakhala ku manda, ndipo panalibe amene akanatha kumumanganso ngakhale ndi unyolo. Pakuti nthawi zambiri akamumanga manja ndi miyendo amadula maunyolo ndi kudula zitsulo zimene zinali mʼmapazi ake. Panalibe amene anali ndi mphamvu yoti ndi kumugonjetsa. Usana ndi usiku ankakhala ku manda ndi kumapiri, akulira ndi kudzicheka ndi miyala.
Ataona Yesu ali patali, anathamanga nagwa pa mawondo ake pamaso pake. Iye anafuwula kwambiri nati, “Mukufuna muchite nane chiyani, Yesu Mwana wa Mulungu Wammwambamwamba? Lumbirani kwa Mulungu kuti simundizunza!” Pakuti Yesu anati kwa iye, “Tuluka mwa munthuyu, iwe mzimu woyipa!”
Ndipo Yesu anamufunsa iye, “Dzina lako ndani?”
Iye anayankha kuti, “Dzina langa ndine Legiyo, pakuti tilipo ambiri.” Ndipo anamupempha Yesu mobwerezabwereza kuti asazitulutse mʼderalo.
Gulu lalikulu la nkhumba limadya mʼmbali mwa phiri limene linali pafupi. Ziwandazo zinapempha Yesu kuti, “Titumizeni pakati pa nkhumbazo; ndipo mutilole tilowe mwa izo.” Iye anazipatsa chilolezo, ndipo mizimu yoyipayo inatuluka ndi kukalowa mu nkhumbazo. Gulu la nkhumba, zokwana pafupifupi 2,000 zinathamanga kutsetserekera ku nyanja ndipo zinamira.
Omwe amaweta nkhumbazo anathawa ndi kukawuza anthu za izi mu mzinda ndi ku madera a ku midzi, ndipo anthu anapita kukaona zomwe zinachitika. Atafika kwa Yesu, anaona munthu amene anagwidwa ndi ziwanda zambiri uja atakhala pansi pomwepo, atavala, ndipo ali bwinobwino. Iwo anachita mantha. Amene anaona zimenezi anawuza anthu zomwe zinachitika kwa munthu wogwidwa ndi ziwandayo ndipo anawawuzanso za nkhumbazo. Ndipo anthu anayamba kumupempha Yesu kuti achoke mʼdera lawo.
Yesu akulowa mʼbwato, munthu amene anagwidwa ndi ziwanda uja anamupempha kuti apite nawo. Yesu sanamulole, koma anati, “Pita kwanu ku banja lako ndipo ukawawuze zimene Ambuye wakuchitira, ndi chifundo chimene wakuchitira.” Pomwepo munthuyo anapita nayamba kuwuza anthu a ku Dekapoli zinthu zimene Yesu anamuchitira. Ndipo anthu onse anadabwa.
Mtsikana Womwalira ndi Mayi Wodwala
Yesu atawolokeranso pa bwato kupita mbali ina ya nyanja, gulu lalikulu la anthu linasonkhana momuzungulira. Ali mʼmbali mwa nyanja, mmodzi wa akulu a mʼsunagoge, dzina lake Yairo anafika pamenepo. Ataona Yesu, anagwa pa mapazi ake, ndi kumudandaulira kwambiri nati, “Mwana wanga wamkazi wamngʼono ali pafupi kufa. Chonde tiyeni kuti mukamusanjike manja kuti akachiritsidwe nakhala ndi moyo.” Ndipo Yesu anapita naye.
Gulu lalikulu la anthu linamutsata ndi kumamupanikiza Iye. Pomwepo panali mayi amene amadwala nthenda yotaya magazi kwa zaka khumi ndi ziwiri. Iye anavutika kwambiri pamene asingʼanga ambiri ankamusamalira ndipo anagwiritsa ntchito zonse anali nazo, koma mʼmalo mochira, nthenda yake inkakulakulabe. Atamva za Yesu, anabwera kumbuyo kwake mʼgulu la anthu ndipo anakhudza mkanjo wake, chifukwa anaganiza kuti, “Ngati nditangokhudza mkanjo wake, ndidzachiritsidwa.” Nthawi yomweyo magazi ake analeka kutuluka ndipo anamva mʼthupi mwake kuti wamasulidwa ku vuto lake.
Pomwepo Yesu anazindikira kuti mphamvu inachoka mʼthupi mwake. Anatembenuka mʼgulu la anthu ndipo anafunsa kuti, “Ndani wakhudza zovala zanga?”
Ophunzira ake anayankha kuti, “Mukuona kuti anthu akukupanikizani, ndipo Inu mukufunsa kuti, ‘Ndani wandikhudza?’ ”
Koma Yesu anapitirizabe kuyangʼana kuti aone amene anachita zimenezi. Kenaka mayi uja pozindikira chimene chinamuchitikira, anabwera ndi kugwa pa mapazi ake, ndipo akunjenjemera ndi mantha, anamuwuza zoona zokhazokha. Anati kwa iye, “Mwana wamkazi, chikhulupiriro chako chakuchiritsa. Pita mu mtendere ndipo khala womasulidwa ku mavuto ako.”
Pamene Yesu ankayankhulabe, amuna ena anafika kuchokera ku nyumba ya Yairo, mkulu wa sunagoge. Iwo anati, “Mwana wanu wamkazi wamwalira, muvutitsiranjinso aphunzitsiwa?”
Posasamala zomwe ananena, Yesu anamuwuza mkulu wa sunagoge uja kuti, “Usachite mantha; ingokhulupirira.”
Iye sanalole munthu wina aliyense kuti amutsatire koma Petro, Yakobo ndi Yohane mʼbale wa Yakobo. Atafika ku nyumba ya mkulu wa sunagoge, Yesu anaona chipiringu cha anthu akulira ndi kufuwula kwambiri. Analowa nati kwa iwo, “Mukuchita phokoso ndi kulira chifukwa chiyani? Mwanayu sanamwalire koma ali mtulo.” Koma anamuseka Iye.
Atawatulutsa onse panja, Iye anatenga abambo ndi amayi ake a mwanayo ndi ophunzira omwe anali naye, ndipo analowa mʼmene munali mwanayo. Anagwira dzanja lake nanena kwa iye, “Talita Kumi!” (Kutanthauza kuti, “Mtsikana, ndikunena ndi iwe, imirira!”) Nthawi yomweyo anayimirira nayenda mozungulira (anali wa zaka khumi ndi ziwiri). Pa ichi onse anadabwa kwambiri. Anawalamulira kwambiri kuti asawuze wina aliyense za ichi, ndipo anawawuza kuti amupatse kanthu koti adye.
Amupeputsa Yesu ku Nazareti
Yesu anachoka kumeneko napita ku mudzi kwawo, pamodzi ndi ophunzira ake. Tsiku la Sabata litafika, anayamba kuphunzitsa mʼsunagoge, ndipo ambiri amene anamumva anadabwa.
Iwo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu anazitenga kuti zimenezi? Kodi ndi nzeru yotani imene munthu ameneyu wapatsidwa, kuti Iye akuchitanso zodabwitsa! Kodi uyu si mpalamatabwa uja? Kodi uyu si mwana wa Mariya ndi mʼbale wa Yakobo, Yose, Yudasi ndi Simoni? Kodi alongo ake si ali ndi ife?” Ndipo anakhumudwa naye.
Yesu anawawuza kuti, “Mneneri amalemekezedwa kulikonse kupatula kwawo, ndi pakati pa abale ake ndi a mʼbanja mwake.” Sanachite zodabwitsa kumeneko, koma anangosanjika manja pa odwala ochepa ndi kuwachiritsa. Ndipo Iye anadabwa chifukwa chakusowa chikhulupiriro kwawo.
Yesu Atuma Ophunzira Khumi ndi Awiri
Pamenepo Yesu anayenda mudzi ndi mudzi kuphunzitsa. Atayitana khumi ndi awiriwo, Iye anawatuma awiriawiri ndipo anawapatsa ulamuliro pa mizimu yoyipa.
Zomwe anawalangiza ndi izi: “Musatenge kanthu ka paulendo koma ndodo yokha; osatenga buledi, thumba, kapena ndalama. Muvale nsapato koma osatenga malaya apadera. Pamene mulowa mʼnyumba mukakhale momwemo kufikira mutachoka mʼmudzimo. Ndipo ngati pa malo ena sakakulandirani kapena kukumverani, sasani fumbi la kumapazi anu pamene mukuchoka, kuti ukhale umboni wowatsutsa.”
Anatuluka kupita kukalalikira kuti anthu atembenuke mtima. Anatulutsa ziwanda zambiri ndi kudzoza mafuta odwala ambiri ndi kuwachiritsa.
Yohane Mʼbatizi Adulidwa Mutu
Mfumu Herode anamva zimenezi, pakuti dzina la Yesu linali litadziwika kwambiri. Ena amati, “Yohane Mʼbatizi waukitsidwa kwa akufa, ndipo nʼchifukwa chake mphamvu zochita zodabwitsa zinkagwira ntchito mwa Iye.”
Ena anati, “Iye ndi Eliya.”
Enanso anati, “Ndi mneneri, ofanana ndi mmodzi wa aneneri akale.”
Koma Herode atamva zimenezi anati, “Yohane, munthu amene ndinamudula mutu, waukitsidwa kuchokera kwa akufa.”
Pakuti Herode iye mwini analamula kuti amumange Yohane ndi kumuyika mʼndende. Anachita izi chifukwa cha Herodia, mkazi wa mʼbale wake Filipo, amene iye anamukwatira. Pakuti Yohane ankanena kwa Herode kuti, “Sikololedwa kwa inu kuti mukwatire mkazi wa mʼbale wanu.” Ndipo Herodia anamusungira Yohane chidani ndipo anafuna kumupha, koma sanathe kutero, chifukwa Herode anaopa Yohane ndipo anamuteteza, podziwa kuti iye anali munthu wolungama ndi woyera mtima. Herode akamamva Yohane, ankathedwa nzeru; komabe amakonda kumumvetsera.
Pomaliza mpata unapezeka. Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwake, Herode anakonzera phwando akuluakulu ake, akulu a ankhondo ndi anthu odziwika a mu Galileya. Mwana wamkazi wa Herodia atabwera ndi kudzavina, anakondweretsa Herode ndi alendo ake a pa mphwandopo.
Mfumu inati kwa mtsikanayo, “Undipemphe chilichonse chimene ukuchifuna, ndipo ndidzakupatsa.” Ndipo analonjeza ndi lumbiriro kuti, “Chilichonse chimene upempha ndidzakupatsa, ngakhale theka la ufumu wanga.”
Iye anatuluka nati kwa amayi ake, “Kodi ndikapemphe chiyani?”
Iye anamuyankha kuti, “Mutu wa Yohane Mʼbatizi.”
Nthawi yomweyo mtsikana uja anafulumira kupita komwe kunali mfumu ndi pempho lake: “Ndikufuna kuti mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.”
Mfumu inamva chisoni chachikulu, koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo ake a pa mphwandolo, sanafune kumukaniza. Nthawi yomweyo iye anatumiza yemwe anali ndi ulamuliro wonyonga anthu kuti abweretse mutu wa Yohane. Munthuyo anapita, nakadula mutu wa Yohane mʼndende, nabweretsa mutuwo mʼmbale. Anawupereka kwa mtsikanayo, ndipo iye anakapereka kwa amayi ake. Atamva izi, ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo ndi kukawuyika mʼmanda.
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
Atumwi anasonkhana mozungulira Yesu namufotokozera zonse zomwe anachita ndi kuphunzitsa. Popeza kuti panali anthu ambiri amene amabwera ndi kumapita, analibe mpata wakuti adye, ndipo Iye anawawuza kuti, “Tiyeni kuno kumalo achete kuti tikapume.”
Ndipo anachoka okha pa bwato napita kumalo a okhaokha. Koma ambiri amene anawaona akuchoka anawazindikira ndipo anathamanga wapansi kuchokera mʼmidzi yonse nakayambirira kufika. Yesu atafika ku mtunda ndi kuona gulu lalikulu la anthu, anamva nawo chisoni chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.
Pa nthawi iyi nʼkuti dzuwa litapendeka, ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kuthengo, ndipo ano ndi madzulo. Awuzeni anthuwa azipita ku midzi ndi madera ozungulira, kuti akadzigulire kanthu kakuti adye.”
Koma Iye anayankha kuti, “Apatseni kanthu koti adye.”
Iwo anati kwa Iye, “Apa pafunika ndalama za miyezi isanu ndi itatu zomwe munthu amalandira! Kodi tipite kukagwiritsa ntchito ndalama zotere kugulira buledi kuti tiwapatse adye?”
Iye anawafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati? Pitani mukaone.”
Ataona anati kwa Iye, “Asanu ndi nsomba ziwiri.”
Pamenepo Yesu anawalamulira kuti awakhazike anthu pansi mʼmagulu pa msipu obiriwira. Ndipo anakhala pansi mʼmagulu a anthu 100 ndi gulu la anthu makumi asanu. Atatenga malofu a buledi asanu ndi nsomba ziwiri, nayangʼana kumwamba, Iye anayamika nagawa malofu a bulediwo. Kenaka anawapatsa ophunzira ake kuti awapatse anthu. Ndipo anagawanso nsomba ziwirizo kwa onse. Onse anadya ndipo anakhuta, ndipo ophunzira ake anatola buledi ndi nsomba zotsalira zokwanira madengu khumi ndi awiri. Chiwerengero cha amuna amene anadya chinali 5,000.
Yesu Ayenda pa Nyanja
Nthawi yomweyo Yesu anawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita ku Betisaida, pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita. Atawasiya, Iye anakwera ku phiri kukapemphera.
Pofika madzulo, bwato linali pakati pa nyanja, ndipo Iye anali yekha pa mtunda. Iye anaona ophunzira ake akuvutika popalasa bwato, chifukwa mphepo imawomba mokumana nawo. Pa nthawi ya mʼbandakucha Iye anafika kwa iwo akuyenda pa nyanja. Anali pafupi kuwapitirira, koma atamuona Iye akuyenda pa nyanja, anaganiza kuti anali mzukwa. Iwo anafuwula, pakuti onse anamuona ndipo anachita mantha.
Nthawi yomweyo Iye anawayankhula nati, “Limbani mtima! Ndine. Musachite mantha.” Ndipo Iye anakwera mʼbwato pamodzi nawo, ndipo mphepo inaleka. Iwo anadabwa kwambiri, popeza sanazindikire zimene zinachitika pa malofu a buledi; pakuti mitima yawo inali yowuma.
Atawoloka, anafika ku Genesareti nayima pa dooko. Atangotuluka mʼbwato, anthu anamuzindikira Yesu. Anathamanga uku ndi uko mʼdera lonse nakanyamula odwala pa machira kupita nawo kulikonse kumene anamva kuti kuli Iye. Ndipo kulikonse kumene anapita, ku midzi, mʼmizinda ndi madera a ku midzi, iwo anayika odwala mʼmalo a mʼmisika. Iwo anamupempha kuti awalole kuti akhudze ngakhale mphonje za mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachira.
Miyambo ya Makolo ya Ayuda
Afarisi ndi ena mwa aphunzitsi amalamulo omwe anachokera ku Yerusalemu anasonkhana momuzungulira Yesu ndipo iwo anaona ophunzira ake akudya chakudya ndi mʼmanja mwakuda kapena kuti mʼmanja mosasamba. (Afarisi ndi Ayuda onse sadya pokhapokha atasamba mʼmanja, kusunga mwambo wa makolo awo. Akabwera kuchokera ku msika samadya pokhapokha atasamba. Ndipo amasunga miyambo ina yambiri monga, kutsuka zikho, mitsuko ndi maketulo).
Choncho Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anafunsa Yesu kuti, “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu satsatira mwambo wa makolo, mʼmalo mwake amangodya chakudya ndi mʼmanja mwakuda?”
Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti:
“Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Amandilambira Ine kwachabe;
ndi kuphunzitsa malamulo ndi malangizo a anthu.
Mwasiya malamulo a Mulungu ndipo mwagwiritsitsa miyambo ya anthu.”
Ndipo anawawuzanso kuti, “Inu muli ndi njira yabwino yokankhira kumbali malamulo a Mulungu kuti mukatsatire miyambo yanuyo! Pakuti Mose anati, ‘Lemekeza abambo ako ndi amayi ako,’ ndipo, ‘aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.’ Koma inu mumati, ngati munthu anena kwa abambo ake kapena amayi ake kuti, ‘Thandizo lililonse mukanayenera kulandira kuchokera kwa ine ndi Korobani’ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa kwa Mulungu), pamenepo inu simumalola kuti achitire kanthu kalikonse abambo kapena amayi ake. Potero mumachepetsa mawu a Mulungu kukhala wopanda mphamvu ndi miyambo yanu imene mumapatsirana. Ndipo mumachita zinthu zina zambiri monga zimenezi.”
Yesu anayitananso gulu la anthu ndipo anati, “Tandimverani nonsenu, ndipo zindikirani izi. Palibe kanthu kunja kwa munthu kamene kakalowa mwa iye kangamusandutse wodetsedwa. Koma zimene zituluka mwa munthu ndizo zimupanga kukhala wodetsedwa.” (Ngati wina ali ndi makutu akumva amve).
Atalisiya gulu la anthu ndi kulowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa za fanizoli Iye anawafunsa kuti, “Kodi nanunso simumvetsetsa? Kodi simukuona kuti palibe kanthu kamene kakalowa mwa munthu kochokera kunja kakhoza kumudetsa? Pakuti sikalowa mu mtima wake koma mʼmimba mwake, ndipo kenaka kamatuluka kunja.” (Ndi mawu amenewa, Yesu anayeretsa zakudya zonse).
Anapitiriza kuti, “Chimene chichokera mwa munthu ndi chomwe chimamudetsa. Pakuti kuchokera mʼkati mwa mitima ya anthu, mumatuluka maganizo oyipa, chiwerewere, kuba, kupha, chigololo, dyera, nkhwidzi, chinyengo, machitidwe onyansa, kaduka, chipongwe, kudzikuza ndi kupusa. Zoyipa zonsezi zimatuluka mʼkati ndipo zimadetsa munthu.”
Chikhulupiriro cha Mayi wa ku Siriya Fonisia
Yesu anachoka kumalo amenewo napita ku madera a Turo. Iye analowa mʼnyumba ndipo sanafune wina kuti adziwe zimenezi; komabe sanathe kudzibisa. Kunena zoona, amayi amene kamwana kawo kakakazi kanali kogwidwa ndi mzimu woyipa, atangomva za Iye, anabwera nagwada pa mapazi ake. Mayiyu anali Mhelene, wobadwira ku Fonisia wa ku Siriya. Anamupempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wake.
Iye anamuwuza kuti, “Choyamba asiye ana adye zimene akuzifuna, pakuti si kwabwino kutenga buledi wa ana ndi kuponyera agalu awo.”
Mayiyo anayankha kuti, “Inde Ambuye, koma ngakhale agalu amadya zomwe zimagwa pansi kuchokera pa tebulo la ana.”
Ndipo Iye anamuwuza kuti, “Chifukwa cha yankholi, ukhoza kupita; chiwanda chachoka mwa mwana wako wamkazi.”
Atapita kwawo anakapeza mwana wake aligone pa bedi, chiwanda chitatuluka.
Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosamva ndi Wosayankhula
Ndipo Yesu anachoka ku dera la Turo nadutsa pakati pa Sidoni, kutsikira ku nyanja ya Galileya kupita ku dera la Dekapoli. Kumeneko anthu ena anabweretsa kwa Iye munthu amene anali wosamva ndi wosayankhula, ndipo anamupempha kuti asanjike dzanja pa iye.
Atamutengera iye pambali, patali ndi gulu la anthu, Yesu analowetsa zala zake mʼmakutu a munthuyo. Kenaka anapaka malovu pachala ndi kukhudza lilime la munthuyo. Iye anayangʼana kumwamba ndipo ndi mawu otsitsa moyo, anati kwa iye, “Efataa!” (Kutanthauza kuti, “Tsekuka!”) Atachita izi, makutu a munthuyo anatsekuka komanso lilime lake linamasuka ndipo anayamba kuyankhula momveka bwino.
Yesu anawalamula kuti asawuze wina aliyense. Koma pamene anapitiriza kuwaletsa, iwo anapitiriza kuyankhula za izi. Anthu anadabwa kwambiri. Iwo anati, “Wachita zonse bwino, ngakhale Iyenso atsekula makutu a osamva ndi osayankhula kuti ayankhule.”
Yesu Adyetsa Anthu 4,000
Mʼmasiku amenewo gulu lina lalikulu la anthu linasonkhana. Popeza iwo analibe chakudya, Yesu anayitana ophunzira ake nati kwa iwo, “Ndili ndi chifundo ndi anthu awa; akhala ali ndi Ine masiku atatuwa ndipo alibe chakudya. Ngati nditawawuza kuti apite kwawo ali ndi njala, iwo adzakomoka mʼnjira chifukwa ena a iwo achokera kutali.”
Ophunzira ake anayankha nati, “Kodi ndi kuti kuthengo kuno kumene munthu angapeze buledi okwanira kuwadyetsa?”
Yesu anafunsa kuti, “Muli ndi malofu a buledi angati?”
Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”
Iye anawuza gulu la anthu kuti likhale pansi. Atatenga malofu a buledi asanu ndi awiri, anayamika, nawanyema ndipo anapatsa ophunzira ake kuti agawire anthu, ndipo iwo anatero. Analinso ndi tinsomba tochepa; Iye anayamikanso chifukwa cha nsombazo. Ndipo anawuza ophunzira kuti awagawire. Anthu anadya ndipo anakhuta. Atamaliza, ophunzira anatola buledi ndi nsomba zotsalira ndi kudzaza madengu asanu ndi awiri. Panali amuna pafupifupi 4,000. Ndipo atawawuza kuti apite kwawo, analowa mʼbwato pamodzi ndi ophunzira ake napita ku dera la Dalamanuta.
Afarisi anabwera nayamba kumufunsa Yesu. Pomuyesa Iye, anamufunsa za chizindikiro chochokera kumwamba. Ndipo anatsitsa moyo nati, “Nʼchifukwa chiyani mʼbado uno ukufuna chizindikiro chodabwitsa? Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe chizindikiro chidzapatsidwa kwa iwo.” Ndipo anawasiya, nalowanso mʼbwato ndi kuwolokera tsidya lina.
Yisiti wa Afarisi ndi Herode
Ophunzira anayiwala kutenga buledi, kupatula buledi mmodzi yekha amene anali naye mʼbwato. Yesu anawachenjeza kuti, “Samalani ndipo onetsetsani yisiti wa Afarisi ndi wa Herode.”
Iwo anakambirana wina ndi mnzake ndipo anati, “Ndi chifukwa choti tilibe buledi.”
Yesu atadziwa zokambirana zawo anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe buledi? Kodi inu simukuonabe kapena kuzindikira? Kodi mitima yanu ndi yowumitsidwa? Kodi muli ndi maso ndipo simukuona, ndi makutu ndipo mukulephera kumva? Kodi simukukumbukira? Pamene ndinagawa malofu asanu a buledi kwa anthu 5,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”
Iwo anayankha kuti, “Khumi ndi awiri.”
“Ndipo pamene ndinagawa malofu asanu ndi awiri a buledi, kwa anthu 4,000, ndi madengu angati amene munatoleramo buledi ndi nsomba zotsalira?”
Iwo anayankha kuti, “Asanu ndi awiri.”
Iye anawafunsa kuti, “Kodi simumvetsetsabe?”
Kuchiritsidwa kwa Munthu Wosaona ku Betisaida
Iwo anafika ku Betisaida, ndipo anthu ena anabweretsa munthu wosaona ndipo anamupempha Yesu kuti amukhudze. Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo napita naye kunja kwa mudzi. Atalavulira mʼmaso a munthuyo ndi kumusanjika manja, Yesu anafunsa kuti, “Kodi ukuona kalikonse?”
Iye anakweza maso nati, “Ndikuona anthu; akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.”
Kenakanso Yesu anayika manja ake mʼmaso a munthuyo. Ndipo maso ake anatsekuka, naonanso, ndipo anaona zonse bwinobwino. Yesu anamuwuza kuti apite kwawo nati, “Usapite mʼmudzimo.”
Petro Avomereza Khristu
Yesu ndi ophunzira ake anapita ku midzi yozungulira Kaisareya wa Filipo. Ali panjira, Iye anawafunsa kuti, “Kodi anthu amati ndine yani?”
Iwo anayankha kuti, “Ena amati Yohane Mʼbatizi; ena amati Eliya; ndipo enanso amati ndinu mmodzi wa aneneri.”
Iye anafunsa kuti, “Koma nanga inu, mumati ndine yani?”
Petro anayankha kuti, “Inu ndinu Khristu.”
Yesu anawachenjeza kuti asawuze wina aliyense za Iye.
Yesu Aneneratu za Imfa Yake
Iye anayamba kuwaphunzitsa kuti, “Mwana wa Munthu ayenera kumva zowawa zambiri ndi kukanidwa ndi akulu a ansembe, ndi aphunzitsi a malamulo, ndi kuti ayenera kuphedwa ndipo patatha masiku atatu adzaukanso.” Izi anaziyankhula momveka bwino, ndipo Petro anamutengera pambali ndipo anayamba kumudzudzula.
Koma Yesu atatembenuka ndi kuyangʼana ophunzira ake, anamudzudzula Petro nati, “Choka pamaso panga Satana! Suganizira zinthu za Mulungu koma za anthu.”
Njira ya Mtanda
Kenaka anayitana gulu la anthu pamodzi ndi ophunzira ake nati: “Ngati wina aliyense afuna kunditsata Ine, ayenera kudzikana yekha ndi kunyamula mtanda wake ndi kunditsata. Pakuti aliyense amene afuna kupulumutsa moyo wake adzawutaya, koma aliyense amene ataya moyo wake chifukwa cha Ine ndi cha Uthenga Wabwino, adzawupulumutsa. Kodi munthu adzapindulanji akalandira dziko lonse lapansi, koma ndi kutaya moyo wake? Kapena nʼchiyani chomwe munthu angapereke chosinthana ndi moyo wake? Ngati wina achita manyazi chifukwa cha Ine ndi mawu anga mu mʼbado uno wachigololo ndi wochimwa, Mwana wa Munthu adzachita naye manyazi pamene adzabwera mu ulemerero wa Atate ake pamodzi ndi angelo oyera.”
Ndipo anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ena amene ayimirira pano sadzafa asanaone ufumu wa Mulungu ukubwera mwa mphamvu.”
Maonekedwe a Ulemerero wa Yesu pa Phiri
Patatha masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane nawatsogolera kupita ku phiri lalitali, kumene anali okhaokha. Kumeneko maonekedwe ake anasinthika pamaso pawo. Zovala zake zinawala monyezimira kwambiri, kotero kuti palibe sopo wina aliyense amene angaziyeretse monyezimira chotere pa dziko la pansi. Ndipo anaonekera Eliya ndi Mose pamaso pawo, amene ankayankhulana ndi Yesu.
Petro anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, ndi kwabwino kuti ife tili pano. Tiyeni timange misasa itatu; umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.” (Iye sanadziwe choti anene, anali ndi mantha akulu).
Pamenepo mtambo unaoneka ndi kuwaphimba, ndipo mawu anamveka kuchokera mu mtambo kuti, “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa. Mvereni Iye!”
Mwadzidzidzi, atayangʼanayangʼana, sanaonenso wina aliyense ali ndi iwo kupatula Yesu.
Pamene ankatsika kuchokera ku phiri, Yesu anawalamulira kuti asawuze aliyense zimene anaona mpaka Mwana wa Munthu atauka kwa akufa. Iwo anayisunga nkhaniyo nakambirana za tanthauzo lake la “Kuuka kwa akufa.”
Ndipo anamufunsa Iye kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kuyamba wabwera?”
Yesu anayankha kuti, “Kunena motsimikiza, Eliya ayeneradi kuyamba kubwera kudzakonzanso zinthu zonse. Nʼchifukwa chiyani tsono zinalembedwa, kuti Mwana wa Munthu ayenera kuvutika kwambiri ndi kukanidwa? Koma ndikuwuzani, kuti Eliya wabweradi, ndipo amuchitira iye zonse zimene iwo anafuna, monga momwe zalembedwera za iye.”
Kuchiritsidwa kwa Mnyamata Wogwidwa ndi Mzimu Woyipa
Atafika kwa ophunzira ena aja, anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndi aphunzitsi amalamulo akutsutsana nawo. Nthawi yomweyo anthu onse atamuona, anadabwa kwambiri ndipo anathamanga kukamulonjera.
Iye anafunsa kuti, “Mukukangana nawo chiyani iwowa?”
Munthu wina mʼgululo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndinakubweretserani mwana wanga wamwamuna, amene ndi ogwidwa ndi mzimu umene umamulepheretsa kuyankhula. Nthawi iliyonse ukamugwira umamugwetsa pansi. Amatuluka thovu kukamwa, amakukuta mano ake ndipo amawuma. Ndinapempha ophunzira anu kuti awutulutse mzimuwo, koma sanathe.”
Yesu anayankha kuti, “Haa! Mʼbado osakhulupirira, kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Mubweretseni kwa Ine mnyamatayo.”
Ndipo anamubweretsa kwa Iye. Mzimu woyipawo utaona Yesu, nthawi yomweyo unamukomola mnyamatayo. Anagwa pansi ndi kumagubuduka, ndi kuchita thovu kukamwa.
Yesu anafunsa abambo a mnyamatayo kuti, “Kodi wakhala chotere nthawi yayitali bwanji?”
Iye anayankha kuti, “Kuyambira ali wamngʼono, wakhala ukumuponya pa moto kapena mʼmadzi kuti umuphe. Koma ngati mungathe kuchita kanthu, tichitireni chifundo ndipo mutithandize.”
Yesu anati, “ ‘Ngati mungathe!’ Zinthu zonse ndi zotheka kwa iye amene akhulupirira.”
Nthawi yomweyo abambo a mwanayo anafuwula kuti, “Ndikhulupirira; thandizani kusakhulupirira kwanga!”
Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kumalowo, anadzudzula mzimu woyipawo kuti, “Iwe mzimu wolepheretsa kuyankhula ndi kumva, ndikulamulira tuluka mwa iye ndipo usadzalowenso.”
Mzimuwo unafuwula ndi kumugubuduza kwambiri ndipo unatuluka. Mnyamatayo anaoneka ngati mtembo ndipo ambiri anati, “Wafa.” Koma Yesu anamugwira dzanja ndipo anamuyimiritsa, ndipo anayimirira.
Yesu atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali pa okha kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani ife sitinathe kutulutsa chiwandacho?”
Iye anayankha kuti, “Mtundu uwu umatuluka pokhapokha mwapemphera ndi kusala kudya.”
Yesu aneneratu za Imfa yake Kachiwiri
Anachoka malo amenewo nadutsa ku Galileya. Yesu sanafune kuti wina aliyense adziwe kumene anali, chifukwa amaphunzitsa ophunzira ake. Anati kwa iwo, “Mwana wa Munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu. Adzamupha, ndipo patatha masiku atatu adzauka.” Koma sanazindikire chimene amatanthauza, ndipo anachita mantha kuti amufunse.
Wamkulu Ndani mu Ufumu wa Mulungu?
Anafika ku Kaperenawo. Pamene anali mʼnyumba, anawafunsa kuti, “Kodi mumatsutsana chiyani mʼnjira muja?” Koma anakhala chete chifukwa ali mʼnjira amatsutsana za kuti wamkulu kuposa onse ndani.
Atakhala pansi, Yesu anayitana khumi ndi awiriwo nati, “Ngati wina aliyense afuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza ndi wotumikira onse.”
Anatenga kamwana nakayimiritsa pakati pawo ndipo anawawuza kuti, “Aliyense wolandira mmodzi wa ana angʼono awa mʼdzina langa alandira Ine; ndipo aliyense wolandira Ine salandira Ine koma amene anandituma.”
Wosatsutsana Nafe Athandizana Nafe
Yohane anati, “Aphunzitsi, tinaona munthu akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndipo ife tinamuwuza kuti aleke, chifukwa sanali mmodzi wa ife.”
Yesu anati, “Musamuletse, palibe amene amachita chodabwitsa mʼdzina langa ndipo kenaka nanena zoyipa za Ine, pakuti aliyense amene satsutsana nafe ali mbali yathu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene akupatsani chikho cha madzi mʼdzina langa chifukwa ndinu ake a Khristu, sadzataya konse mphotho yake.”
Zochimwitsa Ena
“Ndipo ngati wina aliyense achimwitsa mmodzi wa ana angʼono awa amene akhulupirira Ine, kukanakhala bwino kwa iye kuti aponyedwe mʼnyanja atamangiriridwa mwala waukulu mʼkhosi mwake. Ngati dzanja lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo ndi dzanja limodzi kusiyana ndi kukhala ndi manja awiri ndi kupita ku gehena, kumene moto wake suzima. (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). Ndipo ngati phazi lako likuchimwitsa, lidule. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa mʼmoyo olumala kusiyana ndi kukhala ndi mapazi awiri ndi kuponyedwa mu gehena. (Kumene mphutsi zake sizifa ndipo moto wake suzima). Ndipo ngati diso lako likuchimwitsa, likolowole. Ndi kwabwino kwa iwe kulowa ufumu wa Mulungu ndi diso limodzi, kusiyana ndi kukhala ndi maso awiri ndi kuponyedwa mu gehena, kumene
“ ‘mphutsi zake sizifa
ndipo moto wake suzima.’
Aliyense adzayesedwa ndi moto.
“Mchere ndi wabwino, koma ngati utasukuluka, mungawukoleretsenso bwanji? Mukhale nawo mchere mwa inu nokha, ndipo mukhale pa mtendere wina ndi mnzake.”
Za Kusudzula
Ndipo Yesu anachoka pamalowo ndi kupita kudera la Yudeya ndi kutsidya la mtsinje wa Yorodani. Magulu a anthu anabweranso kwa Iye, ndipo monga mwachizolowezi chake anawaphunzitsa.
Afarisi ena anabwera kudzamuyesa pomufunsa kuti, “Kodi malamulo amalola kuti mwamuna asiye mkazi wake?”
Iye anayankha kuti, “Kodi Mose anakulamulani chiyani?”
Iwo anati, “Mose amaloleza mwamuna kulemba kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa mkazi.”
Yesu anayankha kuti, “Mose anakulemberani lamulo ili chifukwa chakuwuma kwa mitima yanu. Koma pachiyambi cha chilengedwe, Mulungu ‘analenga iwo, mwamuna ndi mkazi.’ ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ Potero sali awirinso, koma mmodzi. Chifukwa chake chimene Mulungu wachilumikiza pamodzi, munthu wina asachilekanitse.”
Pamene analinso mʼnyumba, ophunzira anamufunsa Yesu za izi. Iye anayankha kuti, “Aliyense amene aleka mkazi wake ndi kukakwatira wina achita chigololo kulakwira mkaziyo. Ndipo akasiya mwamuna wake ndi kukakwatiwa ndi wina, achita chigololo.”
Yesu Adalitsa Ana
Anthu anabweretsa ana kwa Yesu kuti awadalitse, koma ophunzira anawadzudzula. Pamene Yesu anaona zimenezi anayipidwa. Anati kwa iwo, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse, pakuti Ufumu wa Mulungu uli wa onga awa. Ndikukuwuzani choonadi, aliyense amene sadzalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana sadzalowamo.” Ndipo ananyamula ana mʼmanja ake, ndi kuyika manja ake pa iwo nawadalitsa.
Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu
Yesu atanyamuka, munthu wina anamuthamangira nagwa mogwada pamaso pake. Iye anafunsa kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
Yesu anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukunditchula wabwino? Palibe wabwino koma Mulungu yekha. Iwe umadziwa malamulo: ‘Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni wonama, usachite chinyengo, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”
Iye anati, “Aphunzitsi zonsezi ndinazisunga kuyambira ndili mnyamata.”
Yesu anamuyangʼana ndi kumukonda nati, “Ukusowa chinthu chimodzi. Pita, kagulitse zonse zimene uli nazo ndipo kapereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ndipo ukabwere ndi kunditsata Ine.”
Pa chifukwa ichi nkhope yake inagwa. Anachoka ali wachisoni, chifukwa anali ndi chuma chambiri.
Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!”
Ophunzira anadabwa ndi mawu ake. Koma Yesu anatinso, “Ananu, nʼkovutadi kulowa mu ufumu wakumwamba! Ndi kwapafupi kwa ngamira kuti idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kuti alowe mu ufumu wa Mulungu.”
Ophunzira anadabwa kwambiri, ndipo anati kwa wina ndi mnzake, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
Yesu anawayangʼana ndipo anati, “Kwa munthu zimenezi nʼzosatheka, koma osati ndi Mulungu; zinthu zonse zimatheka ndi Mulungu.”
Petro anati kwa Iye, “Ife tasiya zonse ndi kukutsatani!”
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti palibe aliyense amene wasiya nyumba kapena abale kapena alongo kapena amayi kapena abambo kapena ana kapena minda chifukwa cha Ine ndi Uthenga Wabwino adzalephera kulandira 100 (nyumba, abale, alongo, amayi, ana ndi minda, pamodzi ndi mazunzo) mʼbado uno ndi moyo wosatha nthawi ya mʼtsogolo. Koma ambiri amene ndi woyambirira adzakhala omalizira, ndipo omalizira adzakhala oyambirira.”
Yesu Aneneratunso za Imfa Yake
Ali pa ulendo wawo wopita ku Yerusalemu, Yesu ali patsogolo, ophunzira ake anadabwa, ndipo amene amamutsatira amachita mantha. Anatenganso ophunzira ake khumi ndi awiri pa mbali ndipo anawawuza zimene zikamuchitikire Iye. Iye anati, “Ife tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa Munthu adzaperekedwa kwa akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo. Adzamuweruza kuti aphedwe ndipo adzamupereka kwa anthu a mitundu ina, amene adzamuchita chipongwe ndi kumuthira malovu, kumukwapula ndi kumupha. Patatha masiku atatu adzauka.”
Pempho la Yakobo ndi Yohane
Ndipo Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anabwera kwa Iye ndipo anati, “Aphunzitsi, tikufuna kuti mutichitire ife chilichonse chimene tipemphe.”
Iye anafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndikuchitireni chiyani?”
Iwo anayankha kuti, “Timafuna kuti mmodzi wa ife adzakhale kumanja ndi wina kumanzere mu ulemerero wanu.”
Yesu anati, “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwere chikho chimene ndidzamwera kapena kubatizidwa ndi ubatizo umene ndibatizidwe nawo?”
Iwo anayankha kuti, “Tikhoza.” Yesu anawawuza kuti, “Mudzamweradi chikho chimene Ine ndidzamwera, ndi kubatizidwa ndi ubatizo umene Ine ndidzabatizidwe nawo, koma kukhala kumanja kapena kumanzere si Ine wopereka. Malo awa ndi a amene anasankhidwiratu.”
Ophunzira khumiwo otsalawo atamva izi anapsera mtima Yakobo ndi Yohane. Yesu anawayitana pamodzi nati, “Inu mukudziwa kuti iwo amene amadziyesa ngati atsogoleri a anthu amitundu ina amadyera anthu awo masuku pamutu. Akuluakulu awonso amaonetsadi mphamvu zawo pa iwo. Sizili choncho ndi inu. Mʼmalo mwake, amene akufuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala wotumikira, ndipo aliyense amene akufuna kukhala wamkulu akhale kapolo wa onse. Pakuti ngakhale Mwana wa Munthu sanabwere kudzatumikiridwa, koma kudzatumikira, ndi kupereka moyo wake kuti ukhale dipo la anthu ambiri.”
Bartumeyu Wosaona
Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, “Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
Yesu anayima nati, “Muyitaneni.” Ndipo anamuyitana kuti, “Kondwera! Imirira! Akukuyitana.” Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.
Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?”
Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.”
Yesu anati, “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!” Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.
Yesu Alowa mu Yerusalemu Mwaulemerero
Atayandikira ku Yerusalemu, anafika ku Betifage ndi Betaniya ku phiri la Olivi. Yesu anatuma awiri a ophunzira ake nati kwa iwo, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukamakalowa, mukapeza mwana wabulu atamangiriridwa pamenepo, amene wina aliyense sanakwerepo. Kamumasuleni ndi kubwera naye kuno. Ngati wina aliyense akakufunsani kuti, ‘Mukuchita zimenezi chifukwa chiyani?’ Kamuwuzeni kuti, ‘Ambuye akumufuna ndipo akamutumiza kuno msanga.’ ”
Anapita ndipo anakapeza mwana wabulu ali kunja mu msewu waukulu atamumangirira pa chipata. Pamene anamumasula, anthu ena amene anayima pomwepo anafunsa kuti, “Mukuchita chiyani, kumasula mwana wabuluyo?” Iwo anayankha monga mmene Yesu anawawuzira, ndipo anthu aja anawalola kuti apite. Atafika naye mwana wabulu kwa Yesu, nayika mikanjo yawo pa buluyo, Iye anakwerapo. Anthu ambiri anayala mikanjo yawo pa msewu, pamene ena anayala nthambi zomwe anadula mʼminda. Amene anatsogola ndi iwo amene ankatsatira ankafuwula kuti,
“Hosana!
“Odala Iye amene akudza mʼdzina la Ambuye!”
“Odala ndi ufumu umene ukubwera wa abambo athu Davide!”
“Hosana Mmwambamwamba!”
Yesu analowa mu Yerusalemu napita ku Nyumba ya Mulungu. Anayangʼana zonse, koma popeza kuti nthawi inali itapita, anatuluka kupita ku Betaniya pamodzi ndi khumi ndi awiriwo.
Yesu Atemberera Mkuyu
Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala. Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.
Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu
Atafika ku Yerusalemu, Yesu analowa mʼbwalo lakunja la Nyumba ya Mulungu ndipo anayamba kupirikitsa anthu amene amagula ndi kugulitsa mʼmenemo. Anagubuduza matebulo a osintha ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda, ndipo Iye sanalole aliyense kugulitsa malonda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu. Ndipo pamene ankawaphunzitsa, Iye anati, “Kodi sikunalembedwe kuti, ‘Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero kwa anthu a mitundu yonse?’ Koma inu mwayisandutsa ‘phanga la achifwamba.’ ”
Akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamva izi ndipo anayamba kufuna njira yoti amuphere Iye, pakuti amamuopa, chifukwa gulu lonse la anthu linazizwa ndi chiphunzitso chake.
Pofika madzulo, iwo anatuluka mu mzindamo.
Mkuyu Wofota
Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu. Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”
Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu. Pamene muyimirira kupemphera, ngati muli ndi chifukwa ndi wina, mukhululukireni, kuti Atate anu akumwamba akukhululukireni machimo anu.” (Koma ngati simukhululukirana, ngakhale Atate anu akumwamba sadzakhululukira machimo anu).
Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake
Iwo anafikanso ku Yerusalemu, ndipo pamene Yesu amayenda mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo ndi akuluakulu anabwera kwa Iye. Iwo anafunsa kuti, “Mukuchita izi ndi ulamuliro wanji? Ndipo anakupatsani ulamuliro umenewu ndi ndani?”
Yesu anayankha kuti, “Ndikufunsani funso limodzi. Mundiyankhe, ndipo ndikuwuzani ndi ulamuliro wanji umene ndikuchitira izi. Ubatizo wa Yohane, unali wochokera kumwamba, kapena kwa anthu? Ndiwuzeni.”
Iwo anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Wochokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ Koma ife tikati, ‘Wochokera kwa anthu.’ ” (Amaopa anthu, pakuti aliyense amakhulupirira kuti Yohane analidi mneneri).
Ndipo anamuyankha Yesu kuti, “Sitikudziwa.”
Yesu anati, “Nanenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wanji ndichitira zimenezi.”
Fanizo la Alimi
Kenaka Iye anayamba kuyankhula nawo mʼmafanizo: “Munthu wina analima munda wamphesa. Anamanga mpanda mozungulira, nakumba dzenje lofinyiramo mphesa ndipo anamanga nsanja. Anawubwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita ku dziko lina. Pa nthawi yokolola anatumiza wantchito kwa alimiwo kuti akatenge kuchokera kwa iwo zina mwa zipatso za munda wamphesa. Koma iwo anamugwira, namumenya ndi kumupirikitsa wopanda kanthu. Kenaka anatumizanso wantchito wina kwa iwo. Iwo anamumenya munthuyo pamutu ndipo anamuzunza mochititsa manyazi. Anatumizanso wina, ndipo iwo anamupha. Anatumizanso ena ambiri; ena a iwo anawamenya, ena anawapha.
“Munthu uja anatsala ndi mwana mmodzi, wamwamuna amene amamukonda. Pomaliza anamutumiza mwanayo nati, ‘Adzamuchitira ulemu mwana wanga.’
“Koma alimi aja anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndi mlowamʼmalo. Tiyeni timuphe, ndipo cholowacho chidzakhala chathu.’ Ndipo anamutenga ndi kumupha, ndipo anamuponya kunja kwa munda wamphesa.
“Kodi nanga mwini munda wamphesa adzachita chiyani? Iye adzabwera ndi kupha alimiwo nadzapereka munda wamphesawo kwa ena. Kodi simunawerenge lemba lakuti:
“ ‘Mwala umene amisiri omanga nyumba anawukana
wakhala mwala wa pa ngodya.
Ambuye achita zimenezi,
ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu?’ ”
Ndipo akulu a ansembe, aphunzitsi a malamulo ndi akuluakulu anafunafuna njira yoti amugwirire Iye chifukwa amadziwa kuti anayankhula fanizoli mowatsutsa iwo. Koma amaopa gulu la anthu; ndipo anamusiya napita.
Za Kupereka Msonkho kwa Kaisara
Pambuyo pake anatuma ena a Afarisi ndi Aherode kwa Yesu kuti adzamukole mawu ake. Iwo anabwera kwa Iye nati, “Aphunzitsi, ife tikudziwa kuti Inu ndi munthu amene mumanena zoona. Inu simutengeka ndi anthu, chifukwa simusamala kuti ndi ndani; koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu molingana ndi choonadi. Kodi ndi koyenera kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? Kodi ife tipereke msonkho kapena ayi?”
Koma Yesu anadziwa chinyengo chawo. Iye anafunsa kuti, “Bwanji mukufuna kundipeza chifukwa? Bweretsani ndalama kuti ndiyione.” Iwo anamubweretsera ndalama, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi nkhope iyi ndi ya ndani? Nanga malembawa ndi a ndani?”
Iwo anayankha kuti, “Za Kaisara.”
Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”
Ndipo anazizwa naye.
Za Ukwati ndi Kuuka kwa Akufa
Kenaka Asaduki, amene amati kulibe kuuka kwa akufa, anabwera kwa Iye ndi funso. Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatilembera kuti munthu akamwalira ndi kusiya mkazi wopanda ana, mʼbale wa munthu womwalirayo akuyenera kukwatira mkaziyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. Tsopano panali abale asanu ndi awiri. Woyamba anakwatira namwalira wosabereka ana. Wachiwiri anakwatira mkazi wamasiyeyo, koma iye anamwalira wosabereka mwana. Zinali chimodzimodzi ndi wachitatu. Kunena zoona, palibe ndi mmodzi yemwe wa asanu ndi awiriwo anasiya ana. Pomaliza, mkaziyo anamwaliranso. Pa kuuka kwa akufa, adzakhala mkazi wa yani pakuti anakwatiwa ndi onse asanu ndi awiri?”
Yesu anawafunsa kuti, “Kodi si pamenepa nanga pomwe mumalakwira chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu za Mulungu? Pamene akufa auka, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. Tsopano kunena zakuti akufa amauka, kodi simunawerenge mʼbuku la Mose, pa nkhani yachitsamba choyaka moto, mmene Mulungu anati kwa iye, ‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iye si Mulungu wa anthu akufa, koma wa amoyo. Inu mwalakwitsa kwambiri!”
Lamulo Lalikulu Koposa
Mmodzi wa aphunzitsi amalamulo anabwera namva iwo akukambirana motsutsana. Poona kuti Yesu anawapatsa yankho labwino, anamufunsa Iye kuti, “Mwa malamulo onse, kodi lopambana koposa ndi liti?”
Yesu anayankha kuti, “Lamulo loposa onse ndi ili: ‘Tamvani inu Aisraeli! Yehova Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi! Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse ndi mphamvu zako zonse.’ Lachiwiri ndi ili: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ Palibe lamulo lina loposa amenewa.”
Munthuyo anayankha kuti, “Mwanena bwino Aphunzitsi. Mwalondola ponena kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo palibe wina wofanana naye koma Iye yekha. Kumukonda Iye; ndi mtima wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu zako zonse, ndi kukonda mnansi wako monga iwe mwini, ndi zopambana kuposa zopereka ndi nsembe zopsereza.”
Yesu ataona kuti wayankha mwanzeru, anati kwa iye, “Iwe suli kutali ndi ufumu wa Mulungu.” Ndipo kuyambira pamenepo panalibe ndi mmodzi yemwe anayesa kumufunsanso.
Khristu ndi Mwana wa Yani?
Yesu akuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amanena kuti, ‘Khristu ndi Mwana wa Davide?’ Pajatu Davide mwini wake, poyankhula mwa Mzimu Woyera, ananena kuti,
“Ambuye anati kwa Ambuye anga:
‘Khalani pa dzanja langa lamanja
kufikira nditayika adani anu
pansi pa mapazi anu.’
Davide mwini wake amutchula Iye, ‘Ambuye.’ Nanga angakhale bwanji mwana wake?”
Gulu lalikulu la anthu linamvetsera ndi chisangalalo.
Yesu Achenjeza Anthu za Aphunzitsi a Malamulo
Pamene ankaphunzitsa, Yesu anati, “Samalani ndi aphunzitsi a malamulo. Amakonda kuyendayenda atavala mikanjo ikuluikulu ndi kumalonjeredwa mʼmisika. Ndipo amakhala pa mipando yofunika kwambiri mʼmasunagoge ndi malo aulemu pa maphwando. Amawononga chuma cha akazi amasiye ndiponso amapemphera mapemphero aatali odzionetsera. Anthu oterewa adzalangidwa kwambiri.”
Chopereka cha Mayi Wamasiye
Yesu anakhala pansi moyangʼanana ndi pamene amaperekera zopereka ndipo amaona anthu akupereka ndalama zawo mʼthumba la Nyumba ya Mulungu. Anthu ambiri olemera anaponya ndalama zambiri. Koma mkazi wamasiye, wosauka anabwera ndi kuyikamo tindalama tiwiri ta kopala, tongokwanira theka la ndalama.
Yesu anayitana ophunzira ake nati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mayi wosauka wamasiyeyu waponya zambiri mʼthumbali kuposa ena onsewa. Iwo apereka molingana ndi chuma chawo; koma iye, mwaumphawi wake, wapereka zonse anali nazo ngakhale zoti akanagulira chakudya.”
Zizindikiro za Kutha kwa Masiku Yomaliza
Iye atachoka mʼNyumba ya Mulungu, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Aphunzitsi taonani! Miyala ikuluikulu! Nyumba zikongolerenji!”
Yesu anayankha kuti, “Kodi mukuziona nyumba zikuluzikuluzi? Palibe mwala ndi umodzi pano umene udzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
Yesu atakhala pansi pa phiri la Olivi moyangʼanana ndi Nyumba ya Mulungu, Petro, Yakobo, Yohane ndi Andreya anamufunsa Iye pambali kuti, “Tatiwuzani, izi zidzachitika liti? Nanga chizindikiro chakuti zatsala pangʼono kukwaniritsidwa chidzakhala chiyani?”
Yesu anawawuza kuti, “Chenjerani kuti wina asakunyengeni. Anthu ambiri adzabwera mʼdzina langa, nadzati, ‘Ine ndi Iyeyo,’ ndipo adzanamiza anthu ambiri. Pamene mudzamva zankhondo ndi mbiri zankhondo, musadzadzidzimuke. Zinthu zotere ziyenera kuchitika, koma sikuti chimaliziro chafika kale ayi. Mtundu udzawukira mtundu unzake, ndi ufumu kuwukira ufumu unzake. Kudzakhala zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana, ndi njala. Izi ndi chiyambi chabe cha zowawa monga mayi pobereka.
“Muyenera kukhala tcheru. Mudzaperekedwa ku mabwalo oweruza ndi kukwapulidwa mwankhanza mʼmasunagoge. Mudzayima pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu monga mboni kwa iwo chifukwa cha Ine. Ndipo Uthenga Wabwino uyenera kuyamba walalikidwa kwa anthu a mitundu yonse. Nthawi iliyonse pamene mwamangidwa ndi kuyimbidwa mlandu, musadandaule za zimene mudzanena. Zimene mudzapatsidwe pa nthawiyo yankhulani; pakuti sindinu amene mudzayankhula, koma Mzimu Woyera.
“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe, ndipo abambo adzapereka mwana wawo. Ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine, koma amene adzalimbika mpaka potsiriza, ameneyo ndiye adzapulumuke.
“Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri. Aliyense amene ali pa denga la nyumba yake asatsike kapena kulowa mʼnyumba kukatenga kanthu kalikonse. Aliyense amene ali ku munda asabwerere kukatenga mkanjo wake. Kudzakhala koopsa mʼmasiku amenewo kwa amayi oyembekezera ndi amayi oyamwitsa! Pempherani kuti zimenezi zisadzachitike nthawi yozizira, chifukwa masiku amenewo adzakhala owawitsa osafanana ndi ena kuyambira pachiyambi, pamene Mulungu analenga dziko, kufikira lero ndipo sadzafanananso ndi ena. Ambuye akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwiratu, amene anawasankha, Iye anawafupikitsa. Pa nthawi imeneyo, ngati wina adzati kwa inu, ‘Taonani, Khristu ali kuno, kapena, Taonani, uyo ali apoyo!’ musakhulupirire. Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero. Choncho khalani tcheru; ndakuwuzani zonse nthawi isanafike.
“Koma masiku amenewo, masautsowo atatha,
“ ‘dzuwa lidzada,
ndipo mwezi sudzawala;
nyenyezi zidzagwa kuchokera ku thambo,
ndipo mayiko mumlengalenga adzagwedezeka!’
“Nthawi imeneyo anthu adzaona Mwana wa Munthu akubwera mʼmitambo ndi mphamvu yayikulu ndi ulemerero. Ndipo adzatuma angelo ake kukasonkhanitsa osankhidwiratu ake ku mphepo zinayi, kuyambira kumalekezero a dziko lapansi mpaka ku malekezero ake enanso.
“Tsopano phunzirani phunziro ili kuchokera ku mtengo wamkuyu. Pamene msonga za nthambi zake zikhala za nthete ndipo masamba ake ayamba kuphukira, mumadziwa kuti dzinja layandikira. Momwenso pamene muona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti wayandikira, ali pa khomo. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti mʼbado uno sudzatha mpaka zinthu zonsezi zitachitika. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzatha, koma mawu anga sadzatha.”
Tsiku ndi Ora Sizikudziwika
“Palibe amene akudziwa za tsikulo kapena nthawi, ngakhale angelo akumwamba, kapena Mwana, koma Atate wokha. Khalani maso! Khalani tcheru! Simudziwa pamene nthawi imeneyo idzafike. Zili ngati munthu amene akuchokapo. Amasiyira nyumba yake antchito ake, aliyense ndi ntchito yake; ndi kumuwuza wa pa khomo kuti azikhala maso.
“Inunso muyenera kukhala maso chifukwa simukudziwa nthawi imene mwini nyumba adzabwere, kaya madzulo, kapena pakati pa usiku, kapena tambala akulira, kapena mʼbandakucha. Ngati atabwera mwadzidzidzi, asadzakupezeni inu muli mtulo. Zimene ndikunena kwa inu, ndikunena kwa aliyense: ‘Khalani tcheru!’ ”
Yesu Adzozedwa ku Betaniya
Tsopano panali patatsala masiku awiri okha kuti tsiku la Paska ndi Phwando la Buledi wopanda yisiti lifike, ndipo akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ankafunafuna mpata woti amugwire Yesu ndi kumupha. Iwo anati, “Koma osati nthawi yaphwando, chifukwa anthu angachite chiwawa.”
Pamene Iye anali mʼBetaniya, atakhala pa tebulo akudya mʼnyumba ya munthu wodziwika kuti Simoni wakhate, anabwera mayi ndi botolo la mafuta onunkhira amtengo wapamwamba opangidwa ndi nadi. Anaphwanya botololo nakhuthula mafutawo pa mutu wa Yesu.
Ena mwa iwo amene analipo, anakwiya nati kwa wina ndi mnzake, “Chifukwa chiyani akuwononga mafuta onunkhirawa? Akanatheka kugulitsidwa ndi ndalama zambiri zoposa malipiro a pa chaka ndipo ndalamazo ndi kupatsa osauka.” Ndipo anamudzudzula iye mwaukali.
Yesu anati, “Musiyeni, chifukwa chiyani mukumuvutitsa? Wandichitira Ine chinthu chabwino. Anthu osauka mudzakhala nawo nthawi zonse, ndipo mukhoza kuwathandiza nthawi iliyonse mungafune. Koma simudzakhala ndi Ine nthawi zonse. Wachita zimene akanatha. Wathira mafuta onunkhira pa thupi langa nthawi isanakwane kukonzekera kuyikidwa kwanga mʼmanda. Zoonadi, ndikuwuzani kuti kulikonse kumene Uthenga Wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse, zimene wachitazi zidzanenedwa pomukumbukira iye.”
Kenaka Yudasi Isikarioti, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anapita kwa akulu a ansembe kuti akamupereke Yesu. Iwo anakondwa pakumva zimenezi ndipo analonjeza kumupatsa iye ndalama. Ndipo ankadikira mpata wabwino woti amupereke.
Mgonero wa Ambuye
Pa tsiku loyamba la Phwando la Buledi wopanda yisiti, nthawi imene mwa mwambo inali ya kupha mwana wankhosa wa Paska, ophunzira a Yesu anafunsa Iye kuti, “Mufuna tipite kuti kumene tikakonzekere kuti mukadyere Paska?”
Pamenepo anatumiza awiri mwa ophunzira ake, nawawuza kuti, “Pitani mu mzinda, ndipo mukakumana ndi mwamuna wonyamula mtsuko wa madzi. Kamutsatireni iye. Kawuzeni mwini nyumba imene iye akalowemo kuti, ‘Aphunzitsi akufunsa: kodi chili kuti chipinda changa cha alendo, kumene ndidyere Paska ndi ophunzira anga?’ Iye adzakuonetsani chipinda chachikulu chapamwamba, chokhala kale ndi zonse ndi chokonzedwa kale. Katikonzereni ife Paska kumeneko.”
Ophunzirawo anachoka, napita mu mzindawo ndipo anakapeza zinthu monga mmene Yesu anawawuzira. Choncho anakakonza Paska.
Ndipo kutada Yesu anafika ndi khumi ndi awiriwo. Pamene ankadya pa tebulo Iye anati, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti mmodzi wa inu adzandipereka, mmodzi amene akudya ndi Ine.”
Iwo anamva chisoni, ndipo mmodzi ndi mmodzi anati kwa Iye, “Kodi ndine?”
Iye anayankha kuti, “Ndi mmodzi mwa khumi ndi awirinu, amene akusunsa buledi mʼmbale pamodzi ndi Ine. Mwana wa Munthu adzapita monga momwe zinalembedwera za Iye. Koma tsoka kwa munthu amene adzapereka Mwana wa Munthu! Kukanakhala bwino kwa iye akanapanda kubadwa.”
Pamene ankadya, Yesu anatenga buledi, nayamika ndipo anamunyema nagawira ophunzira ake nanena kuti, “Tengani, ili ndi thupi langa.”
Kenaka anatenga chikho, nayamika nachipereka kwa iwo ndipo onse anamweramo.
Iye anawawuza kuti, “Awa ndi magazi anga a pangano amene akhetsedwa chifukwa cha ambiri. Zoonadi, ndikuwuzani kuti sindidzamwanso kuchokera ku chipatso cha mphesa mpaka tsikulo pamene ndidzamwa chatsopano mu ufumu wa Mulungu.”
Atayimba nyimbo, anapita ku phiri la Olivi.
Yesu Aneneratu zakuti Petro Adzamukana
Yesu anati, “Nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa:
“ ‘Kantha Mʼbusa,
ndipo nkhosa zidzabalalika.’
Koma ndikadzauka, ndidzatsogola kupita ku Galileya.”
Petro anati, “Ngakhale onse adzakuthaweni, ine sindidzatero.”
Yesu anayankha kuti, “Zoona ndikukuwuza kuti lero lino, usiku uno, tambala asanalire kawiri, iweyo udzandikana katatu.”
Koma Petro ananenetsa kuti, “Ngakhale kutakhala kufa nanu, ine sindidzakukanani.” Ndipo ena onse ananena chimodzimodzi.
Mu Getsemani
Ndipo anapita ku malo otchedwa Getsemani, ndipo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Khalani pano pamene Ine ndi kupemphera.” Iye anatenga Petro, Yakobo ndi Yohane, ndipo anayamba kumva chisoni kwambiri ndi kuvutika mu mtima. Iye anawawuza kuti, “Moyo wanga wagwidwa ndi chisoni chofa nacho. Khalani pano ndipo musagone.”
Atapita patsogolo pangʼono, anagwa pansi ndi kupemphera kuti ngati ndi kotheka oralo limupitirire. Iye anati, “Abba, Atate, zinthu zonse ndi zotheka ndi Inu. Chotsereni chikhochi. Komabe chitani zimene Inu mukufuna, osati zimene Ine ndikufuna.”
Kenaka anabwerera kwa ophunzira ake ndipo anawapeza akugona, Iye anati kwa Petro, “Simoni, kodi uli mtulo? Kodi simukanatha kukhala maso kwa ora limodzi? Khalani tcheru ndi kupemphera kuti musalowe mʼmayesero. Mzimu ukufuna, koma thupi ndi lofowoka.”
Kenakanso anachoka ndi kukapemphera chimodzimodzi. Iye atabwerera, anawapezanso akugona, chifukwa mʼmaso mwawo munadzaza tulo. Iwo sanadziwe choti anene kwa Iye.
Atabweranso kachitatu, anawafunsa kuti, “Kodi mukugonabe ndi kupumula? Pakwana! Nthawi yafika. Taonani, Mwana wa Munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. Nyamukani! Tiyeni tizipita! Uyu wondipereka Ine wafika!”
Amugwira Yesu
Iye akuyankhulabe, Yudasi, mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anatulukira. Anali ndi gulu la anthu litanyamula malupanga ndi zibonga, otumidwa ndi akulu a ansembe, aphunzitsi amalamulo, ndi akuluakulu.
Tsopano womupereka anapangana chizindikiro ndi iwo kuti: “Amene ndikapsompsone ndi iyeyo; mukamugwire ndi kumutenga ali womangidwa.” Atapita kwa Yesu nthawi yomweyo, Yudasi anati, “Aphunzitsi,” ndipo anapsompsona. Anthu anamugwira Yesu ndi kumumanga. Kenaka mmodzi wa iwo amene anayima pafupipo anatulutsa lupanga lake nakhapa wantchito wa wamkulu wa ansembe, nʼkudula khutu lake.
Yesu anati, “Kodi Ine ndikutsogolera gulu lowukira, kuti mubwera ndi malupanga ndi zibonga kudzandigwira? Tsiku ndi tsiku ndinali ndi inu, kuphunzitsa mʼmabwalo a Nyumba ya Mulungu, koma inu simunandigwire. Koma malemba ayenera kukwaniritsidwa.” Pamenepo ophunzira ake onse anathawa namusiya yekha.
Mnyamata wamngʼono amene anangofundira nsalu yokha, wopanda chovala ankamutsatira Yesu. Atamugwira, anathawa wamaliseche kusiya nsalu yake mʼmbuyo.
Yesu ku Bwalo la Milandu
Anamutengera Yesu kwa mkulu wa ansembe, ndipo akulu a ansembe, akuluakulu ndi aphunzitsi amalamulo anasonkhana pamodzi. Petro anamutsatira ali patali, mpaka ku bwalo la mkulu wa ansembe. Kumeneko anakhala pansi ndi alonda namawotha moto.
Akulu a ansembe ndi onse olamulira a Ayuda ankafunafuna umboni womutsutsa Yesu kuti amuphe, koma sanapeze wina uliwonse. Ambiri anamunenera Iye maumboni abodza, koma maumboni awo sanagwirizane.
Kenaka ena anayimirira namunenera umboni wonama womutsutsa Iye kunena kuti, “Tamumva akunena kuti, ‘Ndidzawononga Nyumba ya Mulungu iyi yopangidwa ndi anthu ndipo mʼmasiku atatu ndidzamanga ina, osati yopangidwa ndi munthu.’ ” Ngakhale iwonso umboni wawo sunagwirizane.
Kenaka mkulu wa ansembe anayimirira pakati pawo namufunsa Yesu kuti, “Kodi suyankha? Kodi umboni uwu ndi wotani umene anthu akukuchitira?” Koma Yesu anakhala chete ndipo sanayankhe.
Mkulu wa ansembe anabwereza kumufunsa Iye kuti, “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsikayo?”
Yesu anati, “Ndine, ndipo mudzaona Mwana wa Munthu atakhala kudzanja lamanja la Wamphamvuzonse ndipo akubwera mʼmitambo ya kumwamba.”
Mkulu wa ansembe anangʼamba zovala zaunsembe zake. Iye anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani tikufuna mboni zinanso? Mwamva mwanowo. Muganiza chiyani?”
Onse anavomereza kuti ndi woyenera imfa. Kenaka ena anayamba kumulavulira malovu; anamumanga mʼmaso, namumenya ndi zibakera ndipo anati, “Nenera!” Ndipo asilikali anamutenga namumenya.
Petro Akana Yesu
Petro ali chakumunsi kwa bwalo la milandu, mmodzi wa atsikana a ntchito a mkulu wa ansembe anabwera. Ataona Petro akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa.
Iye anati, “Iwenso unali pamodzi ndi Mnazareti, Yesu.”
Koma iye anakana nati, “Sindikudziwa kapena kumvetsetsa zimene ukuyankhula.” Ndipo anachoka napita ku chipata.
Pamene mtsikana wantchitoyo anamuona iye, anatinso kwa iwo amene anayimirira pomwepo, “Munthu uyu ndi mmodzi mwa iwo.” Anakananso kachiwiri.
Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pafupi anati kwa Petro, “Zoonadi ndiwe mmodzi wa iwo, pakuti ndiwe mu Galileya.”
Iye anayamba kudzitemberera, nalumbira kuti, “Sindimudziwa munthu ameneyu.”
Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Yesu ananena anamuwuza kuti, “Tambala asanalire kawiri, iwe udzandikana katatu.” Ndipo iye anasweka mtima nayamba kulira.
Yesu ku Bwalo la Pilato
Mmamawa, akulu a ansembe pamodzi ndi akuluakulu, aphunzitsi amalamulo ndi olamulira onse anamanga fundo. Anamumanga Yesu, namutenga ndi kukamupereka kwa Pilato.
Pilato anafunsa kuti, “Kodi Iwe ndi Mfumu ya Ayuda?”
Yesu anayankha kuti, “Mwatero ndinu.”
Akulu a ansembe anamunenera zinthu zambiri. Ndipo Pilato anamufunsanso Iye kuti, “Kodi Iwe suyankhapo kanthu? Tamva zinthu zambiri akukunenerazi.”
Koma Yesu sanayankhebe, ndipo Pilato anadabwa.
Pa nthawi ya Phwando, panali chizolowezi chomasula munthu wamʼndende amene anthu amupempha. Munthu wotchedwa Baraba anali mʼndende pamodzi ndi anthu owukira amene anapha anthu pa nthawi ya chipolowe. Gulu la anthu linabwera kwa Pilato ndi kumufunsa kuti awachitire zimene amachita nthawi zonse.
“Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni mfumu ya Ayuda?” Pilato anafunsa, podziwa kuti akulu a ansembe anamupereka Yesu kwa iye chifukwa cha nsanje. Koma akulu a ansembe anasonkhezera anthu kuti Pilato amasule Baraba mʼmalo mwa Yesu.
Pilato anawafunsa kuti, “Kodi nanga ndichite chiyani ndi uyu amene mukumutcha mfumu ya Ayuda?”
Anafuwula kuti, “Mpachikeni!”
Pilato anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani? Wapalamula mlandu wotani?”
Koma anafuwula kwambiri, “Mpachikeni!”
Pilato pofuna kuwakondweretsa anthuwo, anawamasulira Baraba. Analamula kuti Yesu akwapulidwe mwankhanza, ndipo anamupereka kuti akapachikidwe.
Chipongwe cha Asilikali
Asilikali anamutenga Yesu ndi kupita naye mʼkati mwa nyumba yaufumu (dera lokhalako asilikali a mfumu) ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali. Anamuveka Iye mwinjiro wofiira, kenaka analuka chipewa cha minga ndi kuyika pa mutu pake. Ndipo anayamba kunena kwa lye kuti, “Ulemu kwa inu Mfumu ya Ayuda!” Ndipo anamugogoda pa mutu mobwerezabwereza ndi ndodo ndi kumulavulira. Anamugwadira ndi kumulambira Iye. Ndipo anamuchita chipongwe, anamuvula mwinjiro wofiira uja ndi kumuveka zovala zake. Kenaka anamutenga kuti akamupachike.
Yesu Apachikidwa pa Mtanda
Munthu wina ochokera ku Kurene, Simoni, abambo a Alekisanda ndi Rufasi amadutsa kuchokera ku dziko la kwawo, ndipo anamuwumiriza kuti anyamule mtanda. Anafika naye Yesu pa malo otchedwa Gologota (kutanthauza kuti, malo a bade) Kenaka anamupatsa Iye vinyo wosakaniza ndi mure, koma Iye sanamwe. Ndipo anamupachika Iye. Anachita maere ogawana zovala zake kuti aone chimene aliyense angatenge.
Linali ora lachitatu mmawa pamene anamupachika Yesu. Chikwangwani cholembedwapo mlandu wake chinali choti: mfumu ya ayuda. Achifwamba awiri anapachikidwanso pamodzi ndi Iye, wina kumanja kwake ndi wina kumanzere kwake. (Ndipo malemba anakwaniritsidwa amene amati, “Iye anayikidwa mʼgulu la anthu oyipa).” Amene amadutsa pafupi anamunenera mawu amwano, akupukusa mitu yawo ndi kuti, “Haa! Iwe amene udzawononga Nyumba ya Mulungu ndi kuyimanganso masiku atatu, tsika kuchoka pa mtandapo ndipo udzipulumutse wekha!”
Chimodzimodzinso akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo anamunyoza Iye pakati pawo. Iwo anati, “Anapulumutsa ena, koma sangathe kudzipulumutsa yekha! Musiyeni Khristu, Mfumu ya Aisraeli, atsike tsopano kuchoka pa mtanda, kuti ife tione ndi kukhulupirira.” Iwonso amene anapachikidwa naye pamodzi anamulalatira.
Imfa ya Yesu
Pa ora lachisanu ndi chimodzi masana mdima unabwera pa dziko lonse mpaka pa ora lachisanu ndi chinayi masana. Pa ora lachisanu ndi chinayi Yesu analira mofuwula kuti, “Eloi, Eloi, lama sabakitani?” Kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji Ine?”
Ena amene anali pafupi atamva izi anati, “Tamverani, akuyitana Eliya.”
Munthu wina anathamanga, natenga chinkhupule atachiviyika mu vinyo wosasa, anachizika ku mtengo, ndi kumupatsa Yesu kuti amwe. Munthuyo anati, “Musiyeni yekha tsopano. Tiyeni tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”
Ndi mawu ofuwula, Yesu anapuma komaliza.
Chinsalu chotchinga cha mʼNyumba ya Mulungu chinangʼambika pakati kuyambira pamwamba mpaka pansi. Ndipo Kenturiyo, amene anayima patsogolo pa Yesu, atamva kulira kwake ndi kuona mmene anafera anati, “Zoonadi, uyu anali Mwana wa Mulungu.”
Amayi ena anali patali kuonerera. Pakati pawo panali Mariya Magadalena, Mariya amayi a Yakobo wamngʼono ndi Yose ndi Salome. Amayi awa ankamutsatira Iye mu Galileya ndi kumutumikira Iye pa zosowa zake. Amayi enanso ambiri amene anabwera naye ku Yerusalemu analinso pomwepo.
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
Linali Tsiku Lokonzekera (kunena kuti, tsiku lomwe limatsatizana ndi Sabata). Choncho madzulo atayandikira, Yosefe wa ku Arimateyu, mkulu wolamulira odziwika bwino, amene amadikirira ufumu wa Mulungu, anapita kwa Pilato molimba mtima ndi kukapempha mtembo wa Yesu. Pilato anadabwa pakumva kuti anali atamwalira kale. Anayitana Kenturiyo, namufunsa ngati Yesu anali atamwalira kale. Atawuzidwa ndi Kenturiyo kuti zinali motero, anapereka mtembowo kwa Yosefe. Choncho Yosefe anagula nsalu yabafuta, natsitsa thupi, ndipo analikulunga mʼnsalu, naliyika mʼmanda amene anawagoba pa mwala. Kenaka anagubuduza mwala umene anatseka nawo mandawo. Mariya Magadalena ndi Mariya amayi a Yose anaona kumene anamuyika Yesu.
Kuuka kwa Yesu
Litapita tsiku la Sabata, Mariya Magadalena, ndi amayi ake a Yakobo, ndi Salome anagula zonunkhiritsa ndi cholinga chakuti apite akadzoze thupi la Yesu. Mmamawa, tsiku loyamba la Sabata, dzuwa litangotuluka kumene, anali pa ulendo wopita ku manda ndipo anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi akatikugudubuzira mwala pa khomo la manda ndani?”
Koma atakweza maso awo, anaona kuti mwala umene unali waukulu kwambiri wagubuduzidwa kale. Atalowa mʼmanda, anaona mnyamata atavala mwinjiro woyera atakhala ku mbali ya kumanja, ndipo iwo anachita mantha.
Iye anati, “Musaope. Kodi mukufuna Yesu wa ku Nazareti, amene anapachikidwa? Wauka! Sali muno. Onani malo amene anamugonekapo. Koma pitani, kawuzeni ophunzira ake ndi Petro kuti, ‘Iye watsogola kupita ku Galileya. Kumeneko mukamuona Iye monga momwe anakuwuzirani.’ ”
Akunjenjemera ndi kudabwa, amayiwo anatuluka ndipo anathawa ku mandako. Sananene china chilichonse kwa aliyense, chifukwa anachita mantha.
[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe vesi 9 mpaka 20.]
Yesu Aonekera kwa Mariya Magadalena
Yesu atauka kwa akufa mmawa pa tsiku loyamba la Sabata, anayamba kuonekera kwa Mariya Magadalena, amene anatulutsa mwa iye ziwanda zisanu ndi ziwiri. Iye anapita ndi kukawawuza amene anali ndi Yesu, amene ankakhuza maliro ndi kulira. Atamva kuti Yesu ali moyo ndikuti amuona, iwo sanakhulupirire.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira Awiri
Zitatha izi Yesu anaonekera mʼmaonekedwe ena kwa awiri a iwo amene anali ku dera la ku mudzi. Iwo anabwerera ndi kudzawawuza enawo; koma iwo sanakhulupirirebe.
Yesu Ayankhula kwa Ophunzira Khumi ndi Mmodzi
Pambuyo pake Yesu anaonekera kwa khumi ndi mmodziwo pamene ankadya; anawadzudzula chifukwa chopanda chikhulupiriro ndi kukanitsitsa kwawo kuti akhulupirire amene anamuona Iye atauka.
Anati kwa iwo, “Pitani mʼdziko lonse lapansi ndipo mukalalikire Uthenga Wabwino kwa zolengedwa zonse. Aliyense amene akakhulupirire nabatizidwa adzapulumuka, koma amene sakakhulupirira adzalangidwa. Tsono zizindikiro izi zidzawatsata amene adzakhulupirira: Mʼdzina langa adzatulutsa ziwanda; adzayankhula malilime atsopano; adzanyamula njoka ndi manja awo; ndipo pamene adzamwa mankhwala akupha, sadzawapweteka nʼpangʼonongʼono pomwe; adzasanjika manja awo pa anthu odwala ndipo odwalawo adzachira.”
Yesu Apita Kumwamba
Ambuye Yesu atatha kuyankhulana nawo, anatengedwa kupita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu. Pamenepo ophunzira aja anapita ndi kukalalikira ponseponse, ndipo Ambuye anagwira nawo ntchito pamodzi, ndipo anatsimikizira mawuwo ndi zizindikiro zimene ankachita.