- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 MIKA Mika Mika Mik Mika Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu. Tamverani, inu anthu a mitundu yonse, mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo, pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani, Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika. Chiweruzo cha Samariya ndi Yerusalemu Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake; Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi. Mapiri akusungunuka pansi pake, ndipo zigwa zikugawikana ngati phula pa moto, ngati madzi ochokera mʼphiri. Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo, chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli. Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani? Kodi si Samariya? Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati? Kodi si Yerusalemu? “Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja, malo odzalamo mphesa. Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa ndipo ndidzafukula maziko ake. Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya; mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto; ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake. Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere, mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.” Kulira ndi Kumva Chisoni Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni; ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche. Ndidzafuwula ngati nkhandwe ndi kulira ngati kadzidzi. Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika; chafika ku Yuda. Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga, mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo. Musanene zimenezi ku Gati; musalire nʼkomwe. Mugubuduzike mu fumbi ku Beti-Leafura. Inu anthu okhala ku Safiro, muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi. Iwo amene akukhala ku Zanaani sadzatuluka. Beti-Ezeli akulira mwachisoni; chitetezo chake chakuchokerani. Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu, akuyembekezera thandizo, chifukwa Yehova wabweretsa tsoka, lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu. Inu anthu okhala ku Lakisi mangani akavalo ku magaleta. Inu amene munayamba kuchimwitsa mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti zolakwa za Israeli zinapezeka pakati panu. Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana ndi a ku Moreseti Gati. Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama kwa mafumu a Israeli. Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu okhala mu Maresa. Ulemerero wa Israeli udzafika ku Adulamu. Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira ana anu amene mumawakonda; mudzichititse dazi ngati dembo, pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo. Zokonzekera za Munthu ndi Zokonzekera za Mulungu Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu, kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo! Kukacha mmawa amakachitadi chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo. Amasirira minda ndi kuyilanda, amasirira nyumba ndi kuzilanda. Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo, munthu mnzawo kumulanda cholowa chake. Nʼchifukwa chake Yehova akuti, “Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa, tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha. Inu simudzayendanso monyada, pakuti idzakhala nthawi ya masautso. Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe; adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro: ‘Tawonongeka kotheratu; dziko la anthu anga lagawidwa. Iye wandilanda! Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ” Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova kuti agawe dziko pochita maere. Aneneri Onyenga Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere! Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi; ife sitidzachititsidwa manyazi.” Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena: “Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya? Kodi Iye amachita zinthu zotere?” “Kodi mawu ake sabweretsa zabwino kwa amene amayenda molungama? Posachedwapa anthu anga andiwukira ngati mdani. Mumawavula mkanjo wamtengowapatali anthu amene amadutsa mosaopa kanthu, monga anthu amene akubwera ku nkhondo. Mumatulutsa akazi a anthu anga mʼnyumba zawo zabwino. Mumalanda ana awo madalitso anga kosatha. Nyamukani, chokani! Pakuti ano si malo anu opumulirapo, chifukwa ayipitsidwa, awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso. Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti, ‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri, woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’ Alonjeza Chipulumutso “Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse; ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli. Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola, ngati ziweto pa msipu wake; malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu. Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo; iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka. Mfumu yawo idzawatsogolera, Yehova adzakhala patsogolo pawo.” Atsogoleri ndi Aneneri Adzudzulidwa Ndipo ine ndinati, “Tamverani, inu atsogoleri a Yakobo, inu olamulira nyumba ya Israeli. Kodi sindinu oyenera kudziwa kuweruza molungama, inu amene mumadana ndi zabwino ndi kukonda zoyipa; inu amene mumasenda khungu la anthu anga, ndipo mumakungunula mnofu pa mafupa awo; inu amene mumadya anthu anga, mumasenda khungu lawo ndi kuphwanya mafupa awo; inu amene mumawadula nthulinthuli ngati nyama yokaphika?” Pamenepo adzalira kwa Yehova, koma Iye sadzawayankha. Nthawi imeneyo Iye adzawabisira nkhope yake chifukwa cha zoyipa zimene anazichita. Yehova akuti, “Aneneri amene amasocheretsa anthu anga, ngati munthu wina awapatsa chakudya amamufunira ‘mtendere;’ ngati munthu wina sawapatsa zakudya amamulosera zoyipa. Nʼchifukwa chake kudzakuderani, simudzaonanso masomphenya, mdima udzakugwerani ndipo simudzawombezanso. Dzuwa lidzawalowera aneneriwo, ndipo mdima udzawagwera. Alosi adzachita manyazi ndipo owombeza mawula adzanyazitsidwa. Onse adzaphimba nkhope zawo chifukwa Mulungu sakuwayankha.” Koma kunena za ine, ndadzazidwa ndi mphamvu, ndi Mzimu wa Yehova, ndi kulungama, ndi kulimba mtima, kuti ndilalikire za kugalukira kwa Yakobo, kwa Israeli za tchimo lake. Imvani izi, inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo, inu olamulira nyumba ya Israeli, inu amene mumadana ndi kuweruza kolungama; ndipo mumakhotetsa zinthu zonse zolondola; inu amene mukumanga Ziyoni pokhetsa magazi, ndi Yerusalemu ndi kuyipa kwanu. Atsogoleri ake amalandira chiphuphu kuti aweruze, ansembe ake amalandira malipiro kuti alalikire, ndipo aneneri ake amanenera kuti alandire ndalama. Komatu amatsamira pa Yehova nʼkumanena kuti, “Kodi Yehova sali pakati pathu? Palibe tsoka limene lidzatigwere.” Choncho chifukwa cha inu, Ziyoni adzatipulidwa ngati munda, Yerusalemu adzasanduka bwinja, ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira. Phiri la Yehova Mʼmasiku otsiriza, phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse. Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse, ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko. Mayiko ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu. Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo. Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu, ndipo palibe amene adzawachititse mantha, pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula. Mitundu yonse ya anthu itha kutsatira milungu yawo; ife tidzayenda mʼnjira za Yehova Mulungu wathu mpaka muyaya. Cholinga cha Yehova “Tsiku limenelo, Yehova akuti, “ndidzasonkhanitsa olumala; ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa ndiponso amene ndinawalanga. Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala. Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu. Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya. Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga, iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni, ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe; ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.” Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula, kodi ulibe mfumu? Kodi phungu wako wawonongedwa, kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka? Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mayi pa nthawi yake yobereka, pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda ndi kugona kunja kwa mzindawo. Udzapita ku Babuloni; kumeneko udzapulumutsidwa, kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako. Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu yasonkhana kulimbana nawe. Iwo akuti, “Tiyeni timudetse, maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!” Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova; iwo sakuzindikira cholinga chake, Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu. “Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo; ndidzakupatsa ziboda zamkuwa ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.” Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova, chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi. Wolamulira Wochokera ku Betelehemu Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo, pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe. Adzakantha ndi ndodo pa chibwano cha wolamulira wa Israeli. “Koma iwe Betelehemu Efurata, ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda, mwa iwe mudzatuluka munthu amene adzalamulira Israeli, amene chiyambi chake nʼchakalekale, nʼchamasiku amakedzana.” Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire. Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli. Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zake mwa mphamvu ya Yehova, mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake. Ndipo iwo adzakhala mu mtendere, pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi. Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo. Chipulumutso ndi Chiwonongeko Asiriya akadzalowa mʼdziko lathu ndi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa, tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri, ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu. Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga, dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo. Adzatipulumutsa kwa Asiriya akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu kudzatithira nkhondo. Otsalira a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvumbi pa udzu, omwe sulamulidwa ndi munthu kapena kudikira lamulo la anthu. Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu, mʼgulu la anthu a mitundu yambiri, ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango. Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa, amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula, ndipo palibe angathe kuzilanditsa. Mudzagonjetsa adani anu, ndipo adani anu onse adzawonongeka. Yehova akuti, “Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse ndi kuphwasula magaleta anu. Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu ndi kugwetsa malinga anu onse. Ndidzawononga ufiti wanu ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula. Ndidzawononga mafano anu osema pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu; simudzagwadiranso zinthu zopanga ndi manja anu. Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu, ndipo ndidzawononga mizinda yanu. Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiya mitundu imene sinandimvere Ine.” Mlandu wa Yehova ndi Israeli Tamverani zimene Yehova akunena: “Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri; zitunda zimve zimene inu muti muyankhule. Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri; tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi. Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake; Iye akutsutsa Aisraeli. “Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani? Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni. Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo. Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni, pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu. Anthu anga, kumbukirani zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha. Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala, kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.” Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba? Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza, ndi ana angʼombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000, kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta? Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga? Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga? Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino. Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe? Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako. Kulakwa kwa Israeli ndi Chilango chake Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda ndi nzeru kuopa dzina lanu. “Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa. Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo, ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa? Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo, ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake? Anthu ake olemera amachita zachiwawa; anthu ake ndi abodza ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo. Choncho, ndayamba kukuwonongani, kukusakazani chifukwa cha machimo anu. Mudzadya, koma simudzakhuta; mudzakhalabe ndi njala. Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika, chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga. Mudzadzala, koma simudzakolola. Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito. Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake. Inu mwatsatira malangizo a Omuri ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu, ndi khalidwe lawo lonse. Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu; mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.” Chipsinjo cha Israeli Tsoka ine! Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe, pa nthawi yokolola mphesa; palibe phava lamphesa loti nʼkudya, palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri. Anthu opembedza atha mʼdziko; palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala. Anthu onse akubisalirana kuti aphane; aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka. Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa; wolamulira amafuna mphatso, woweruza amalandira ziphuphu, anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna, onse amagwirizana zochita. Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga, munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga. Tsiku limene alonda ako ananena lafika, tsiku limene Mulungu akukuchezera. Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo. Usadalire mnansi; usakhulupirire bwenzi. Usamale zoyankhula zako ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira. Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake, mwana wamkazi akuwukira amayi ake, mtengwa akukangana ndi apongozi ake, adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe. Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo, ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga; Mulungu wanga adzamvetsera. Kuuka kwa Israeli Iwe mdani wanga, usandiseke! Ngakhale ndagwa, ndidzauka. Ngakhale ndikukhala mu mdima, Yehova ndiye kuwunika kwanga. Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova, chifukwa ndinamuchimwira, mpaka ataweruza mlandu wanga ndi kukhazikitsa chilungamo changa. Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika; ndidzaona chilungamo chake. Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi nadzagwidwa ndi manyazi, iye amene anandifunsa kuti, “Ali kuti Yehova Mulungu wako?” Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga; ngakhale tsopano adzaponderezedwa ngati matope mʼmisewu. Idzafika nthawi yomanganso makoma anu, nthawi yokulitsanso malire anu. Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto, ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso. Dziko lapansi lidzasanduka chipululu chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo. Pemphero ndi Matamando Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza, nkhosa zimene ndi cholowa chanu, zimene zili zokha mʼnkhalango, mʼdziko la chonde. Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi monga masiku akale. “Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga, ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.” Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi, ngakhale ali ndi mphamvu zotani. Adzagwira pakamwa pawo ndipo makutu awo adzagontha. Adzabwira fumbi ngati njoka, ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi. Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo; mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu ndipo adzachita nanu mantha. Kodi alipo Mulungu wofanana nanu, amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa za anthu otsala amene ndi cholowa chake? Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika. Inu mudzatichitiranso chifundo; mudzapondereza pansi machimo athu ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja. Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo, ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu, monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu masiku amakedzana.