- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
MALAKI
Malaki
Malaki
Mal
Malaki
Uthenga: Mawu a Yehova kwa Israeli kudzera mwa Malaki.
Ndamukonda Yakobo, Ndamuda Esau
Yehova akuti, “Ine ndakukondani. Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi mwatikonda motani?’ ”
Yehova akuti, “Kodi Esau sanali mʼbale wake wa Yakobo? Komatu Ine ndinakonda Yakobo, koma ndinamuda Esau, ndipo dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu ndipo cholowa chake ndasiyira ankhandwe a mʼchipululu.”
Mwina Edomu nʼkunena kuti, “Ngakhale taphwanyidwa, tidzamanganso mʼmabwinja.”
Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Iwo angathe kumanganso, koma Ine ndidzazigwetsanso. Iwo adzatchedwa dziko loyipa, la anthu amene Yehova wayipidwa nawo mpaka muyaya. Inu mudzaziona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati, ‘Yehova ndi Wamkulu, ukulu wake umafika ngakhale kunja kwa malire a Israeli!’
Nsembe Zosayenera
“Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa.
“Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’
“Inu mwanyoza dzina langa popereka chakudya chodetsedwa pa guwa langa lansembe.
“Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi ife takunyozani bwanji?’
“Mwandinyoza ponena kuti tebulo la Yehova ndi lonyozeka. Mukamapereka nsembe nyama zosaona, kodi sicholakwa? Mukamapereka nsembe nyama zachilema kapena zodwala, kodi sicholakwa? Kayeseni kuzipereka kwa bwanamkubwa wanu! Kodi akasangalatsidwa nanu? Kodi akazilandira? Akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Kodi ndi zopereka zotere mʼmanja mwanu, Iye angakulandireni?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Ndikulakalaka mmodzi wa inu akanatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, kuti musayatsemo moto pachabe pa guwa langa lansembe! Ine sindikukondwera nanu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, “ndipo Ine sindidzalandira zopereka za mʼmanja mwanu. Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’ Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova. “Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ”
Chenjezo kwa Ansembe
“Tsono chenjezo ili ndi la inu, inu ansembe.” Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ngati simumvera, ndipo ngati simulemekeza dzina langa mʼmitima mwanu, ndidzakutembererani ndipo madalitso onse munawalandira ndidzawatemberera. Ndithu, ndawatemberera kale, chifukwa simunalemekeze Ine mʼmitima mwanu.”
“Ine ndidzalanga zidzukulu zanu chifukwa cha inu; ndidzakupakani kumaso ndowe za nsembe zanu zachikondwerero, ndipo ndidzakutayani pamodzi ndi ndowezo.” Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Apo mudzadziwa kuti Ine ndatumiza chenjezoli kuti pangano langa ndi Levi lipitirire. Ine ndinali naye pa pangano, pangano lopatsa moyo ndi mtendere, ndipo ndinamupatsa zimenezi kuti azindiopa, ndipo anandiopadi ndi kulemekeza dzina langa. Pakamwa pake pankatuluka malangizo woona, ndipo pa milomo yake sipanapezeke chinyengo. Iye anayenda nane mwamtendere ndi molungama mtima, ndipo anabweza anthu ambiri mʼnjira zawo zauchimo.
“Pakuti wansembe ayenera kukhala ndi chidziwitso, ndipo anthu ayenera kufunafuna malangizo kuchokera kwa iye, popeza iye ndi mthenga wa Yehova Wamphamvuzonse. Koma inu mwasiya njira yanga ndipo mwapunthwitsa anthu ambiri ndi ziphunzitso zanu; mwayipitsa pangano langa ndi Levi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Choncho Ine ndachititsa kuti munyozedwe ndi kuchititsidwa manyazi pamaso pa anthu onse, chifukwa simunatsate njira zanga koma mwakhala mukuonetsa kukondera pa nkhani za malamulo.”
Kusakhulupirika kwa Yuda
Kodi sitili naye Atate mmodzi tonsefe? Kodi anatilenga si Mulungu mmodzi? Chifukwa chiyani tikudetsa pangano la makolo athu posamakhulupirirana wina ndi mnzake?
Yuda waleka kukhulupirika. Chinthu chonyansa chachitika mu Israeli ndi mu Yerusalemu: Yuda wayipitsa malo opatulika amene Yehova amawakonda, pokwatira mkazi wopembedza mulungu wachilendo. Ndipo wina aliyense wochita zimenezi, kaya munthuyo ndi wotani, Yehova amuchotse ku banja la Yakobo, ngakhale atabweretsa zopereka kwa Yehova Wamphamvuzonse.
China chimene mumachita ndi ichi: Mumakhathamiritsa guwa lansembe la Yehova ndi misozi. Mumalira ndi kufuwula kwambiri chifukwa Iye amakana kuyangʼana nsembe zanu, kapena kulandira mokondwera nsembe za mʼmanja mwanu. Inu mukufunsa kuti, “Chifukwa chake nʼchiyani?” Chifukwa chake nʼchakuti Yehova ndi mboni ya pangano limene unachita ndi mkazi wa unyamata wako, chifukwa sunakhulupirike kwa iye, ngakhale kuti iyeyo ndiye mnzako, ndi mkazi wako mwapangano.
Kodi Yehova sanawalenge iwo ngati munthu mmodzi? Ndi ake mʼthupi ndi mu mzimu. Nʼchifukwa chiyani ali mmodzi? Chifukwa Iye amafuna ana opembedza Mulungu. Motero samala moyo wako wauzimu, ndipo usakhale wosakhulupirika kwa mkazi wa unyamata wako.
Yehova Mulungu wa Israeli akuti, “Ndimadana ndi kulekana ukwati. Ndimadana ndi munthu wochita zankhanza zotere kwa mkazi wake,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Choncho tetezani mzimu wanu, ndipo musakhale osakhulupirika.
Tsiku la Chiweruzo
Mwamutopetsa Yehova ndi zoyankhula zanu.
Inu mukufunsa kuti, “Kodi tamutopetsa bwanji?”
Mwamutopetsa ponena kuti, “Aliyense amene amachita zoyipa ndi wabwino pamaso pa Yehova ndipo iye amakondwera naye” kapena pofunsa kuti, “Ali kuti Mulungu woweruza mwachilungamo?”
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ine ndidzatuma mthenga wanga amene adzakonza njira pamaso panga. Kenaka mwadzidzidzi Ambuye amene mukumufunafuna adzafika ku Nyumba yake. Mthenga wapangano amene mukumuyembekezera adzabwera.”
Koma ndani adzatha kupirira pa tsiku la kubwera kwake? Ndani adzatha kuyima pamene Iye wafika? Pakuti adzakhala ngati moto wa mmisiri wa pa ngʼanjo, kapenanso ngati sopo wa munthu wochapa. Iye adzachita kukhalira pansi ngati mmisiri woyenga ndi woyeretsa siliva. Iye adzayeretsa Alevi ndi kuwayenga ngati golide ndi siliva. Pamenepo Yehova adzakhala ndi anthu amene azidzabweretsa zopereka mwachilungamo, ndipo Yehova adzalandira zopereka za Yuda ndi Yerusalemu, ngati masiku akale, masiku amakedzana.
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Tsono ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Mosataya nthawi ndidzanena mawu otsutsa mfiti, achigololo, a umboni wonama, amene salipira bwino antchito awo, amene amazunza akazi ndi ana amasiye, amene saweruza alendo mwachilungamo, komanso amene sandiopa Ine.”
Kuba za Mulungu
“Ine ndine Yehova, ndipo sindisintha. Choncho inu zidzukulu za Yakobo, simunawonongedwe. Kuyambira nthawi ya makolo anu mwakhala mukuphwanya malamulo anga ndipo simunawatsatire. Bwererani kwa Ine, ndipo Ine ndidzabwerera kwa inu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Tibwerere motani kwa Yehova?’
“Kodi munthu angathe kuba za Mulungu? Komatu inu mumandibera.
“Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi timakuberani motani?’
“Pa zakhumi ndi pa zopereka. Mtundu wanu wonse ndinu otembereredwa, chifukwa mukundibera. Bweretsani chakhumi chathunthu ku nyumba yosungira, kuti mukhale chakudya mʼnyumba mwanga.” Akutero Yehova Wamphamvuzonse, “Tandiyesani, ndipo muone ngati sindidzatsekula zipata zakumwamba, ndi kukugwetserani madalitso ochuluka amene mudzasowe malo owayikamo. Ndidzaletsa tizirombo kuti tisawononge mbewu zanu, ndipo mpesa wa mʼminda mwanu zipatso zake sizidzayoyoka,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Motero anthu amitundu yonse adzakutchulani odala, pakuti dziko lanu lidzakhala lokondweretsa,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Yehova akuti, “Mwayankhula mawu owawa onena za Ine.
“Komabe inu mukufunsa kuti, ‘Kodi tanena chiyani chotsutsana nanu?’
“Mwanena kuti, ‘Kutumikira Mulungu nʼkosapindulitsa. Kodi timapindulanji pochita zofuna zake, ndi kumayenda ngati anamfedwa pamaso pa Yehova Wamphamvuzonse? Koma tsono ife timati anthu odzikuza ndiye odalitsika. Kunena zoona anthu oyipa ndiye amapeza bwino, ngakhale amene amanyoza Mulungu amapulumuka.’ ”
Ndipo woopa Yehova anayamba kukambirana, ndipo Yehova anamvetsera. Buku la chikumbutso linalembedwa pamaso pake, lonena za amene amaopa Yehova ndi kulemekeza dzina lake.
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu amenewo adzakhala anga, tsiku limene Ine ndidzachita izi, adzakhala angaanga. Ndidzawaleka osawalanga monga mmene munthu amachitira chifundo mwana wake amene amamutumikira. Pamenepo mudzaonanso kusiyana pakati pa anthu olungama ndi oyipa, pakati pa amene amatumikira Mulungu ndi amene satumikira Mulungu.”
Tsiku la Yehova
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndithu tsiku likubwera; lidzayaka ngati ngʼanjo. Anthu onse odzikuza, ndi aliyense ochita zoyipa adzapsa ngati chiputu, ndipo pa tsiku limene likubweralo adzapserera ndi moto. Sipadzatsalira muzu kapena nthambi. Koma inu amene mumaopa dzina langa, dzuwa lachilungamo lidzakutulukirani lili ndi kuwala kokuchiritsani. Ndipo inu mudzatuluka ndi kulumphalumpha ngati ana angʼombe amene atulutsidwa mʼkhola. Tsiku limenelo inu mudzapondereza anthu oyipa; adzakhala phulusa ku mapazi anu pa tsiku limene Ine ndidzachite zinthu zimenezi,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Kumbukirani zophunzitsa za mtumiki wanga Mose, malamulo ndi malangizo amene ndinamupatsa pa Horebu kuti awuze Aisraeli onse.
“Taonani, ndidzakutumizirani mneneri Eliya lisanafike tsiku lalikulu ndi loopsa la Yehova. Iye adzabweza mitima ya makolo kwa ana awo, ndi mitima ya ana kwa makolo awo. Kupanda kutero ndidzabwera kudzakantha dziko lanu ndi temberero.”