- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 YOSWA Yoswa Yoswa Yos Yoswa Yehova Asankha Yoswa Kukhala Mtsogoleri Atamwalira Mose mtumiki wa Mulungu, Yehova anati kwa Yoswa mwana wa Nuni mthandizi wa Mose: “Mose mtumiki wanga wamwalira. Ndipo iwe ndi anthu onsewa, tsopano konzekani kuwoloka mtsinje wa Yorodani kupita ku dziko limene ndiwapatse Aisraeli onse. Paliponse pamene phazi lanu liponde, ndikupatsani monga momwe ndinalonjezera Mose. Dziko lanu lidzayambira ku chipululu kummwera mpaka ku mapiri a Lebanoni kumpoto, kuchokeranso ku mtsinje waukulu wa Yufurate kummawa, mpaka dziko lonse la Ahiti, kukafika ku Nyanja Yayikulu ya kumadzulo. Palibe munthu amene adzatha kukugonjetsa masiku onse a moyo wako. Monga Ine ndinakhalira ndi Mose, chomwechonso ndidzakhala nawe. Sindidzakusiya kapena kukataya. “Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima, chifukwa iwe udzatsogolera anthu awa kukalandira dziko limene Ine ndinalonjeza makolo awo kuti ndidzawapatsa. Ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima kwambiri. Usamale ndithu kuti umvere malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anakupatsa. Usachoke pa malamulo anga ndipo kulikonse kumene udzapite udzapambana. Uziwerenga Buku la Malamuloli, uzilingalira zolembedwa mʼmenemo usana ndi usiku, kuti uchite zonse zimene zinalembedwamo. Ukamatero udzapeza bwino ndi kupambana. Paja ndinakulamula kuti ukhale wamphamvu ndi wolimba mtima. Choncho usamachite mantha kapena kutaya mtima popeza Ine Yehova Mulungu wako ndidzakhala nawe kulikonse kumene udzapite.” Tsono Yoswa analamula atsogoleri a Aisraeli nawawuza kuti, “Pitani ku misasa yonse ndipo muwuze anthu kuti, ‘Konzekani, mangani katundu wanu, popeza pakapita masiku atatu kuyambira lero mudzawoloka Yorodani kupita kukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.’ ” Koma Yoswa anawuza fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti, “Kumbukirani zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani kuti, ‘Yehova Mulungu wanu akukupatsani mpumulo, ndi dziko ili kuti likhale lanu.’ Tsono akazi anu, ana anu ndi ziweto zanu zitsale mʼdziko lino limene Mose anakupatsani kummawa kwa Yorodani. Koma ankhondo anu okha ndiwo awoloke atatenga zida zawo ndi kupita patsogolo pa abale anu kukawathandiza. Abale anuwo akadzalandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa monga inu mwachitira, inu mudzabwerera kudzakhazikika mʼdziko lanu limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani tsidya la kummawa kwa Yorodani.” Kenaka iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife tidzachita chilichonse chimene mwatilamula, ndipo kulikonse kumene mudzatitume tidzapita. Monga momwe tinamvera Mose kwathunthu, chomwechonso tidzakumvera iwe. Yehova Mulungu wanu akhale nanu monga momwe anachitira ndi Mose. Aliyense wotsutsana ndi inu kapena wosamvera zimene mutilamula adzaphedwa. Inu mukhale wamphamvu ndi wolimba mtima!” Rahabe ndi Anthu Ozonda Dziko Tsono Yoswa mwana wa Nuni anatuma anthu awiri okazonda dziko mwachinsinsi kuchokera ku Sitimu. Iye anawawuza kuti, “Pitani mukaone dzikolo makamaka mzinda wa Yeriko.” Kotero iwo anapita ndipo anakafika ku nyumba ya mkazi wadama dzina lake Rahabe, ndipo anagona kumeneko. Mfumu ya Yeriko inawuzidwa kuti, “Aisraeli ena afika mu mzinda muno usiku uno kudzazonda dziko.” Choncho Mfumu ya Yeriko inatumiza uthenga kwa Rahabe kuti, “Atulutse anthu amene abwera ku nyumba kwakowo chifukwa iwo abwera kuti adzazonde dzikoli.” Koma pa nthawiyi nʼkuti mkaziyo atatenga amuna awiriwo ndi kuwabisa. Tsono anayankha kuti, “Inde, anthuwo anafikadi ku nyumba kuno. Koma sindinadziwe kumene anachokera. Iwo achoka kuno ndi chisisira, chipata cha mzinda chili pafupi kutsekedwa. Ndiye sindidziwa kumene alowera. Koma mukawalondola msanga muwapeza.” Koma nʼkuti atawakweza pa denga azondiwo ndi kuwabisa pansi pa mapesi a thonje amene iye anawayika pa dengapo. Nthumwi za mfumu zija zitatuluka ndipo chipata chinatsekedwa. Nthumwizo zinapita kukawafunafuna azondi aja mpaka ku dooko la Yorodani. Azondiwo asanagone, Rahabe anakwera pa denga ndipo anawawuza kuti, “Ine ndikudziwa kuti Yehova wakupatsani dziko lino ndipo tili ndi mantha. Anthu onse a mʼdziko lino ali ndi mantha chifukwa cha inu. Ife tinamva mmene Yehova anawumitsira madzi a Nyanja Yofiira inu mukufika pamene munatuluka mʼdziko la Igupto. Tamvanso zimene munachita kwa Sihoni ndi Ogi, mafumu awiri a Aamori amene ali kummawa kwa Yorodani. Inu munawawononga kotheratu. Titamva zimenezi, ife tinataya mtima ndipo aliyense wa ife ali ndi mantha chifukwa cha inu. Tikudziwa kuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. Choncho mulumbire pamaso pa Yehova ndi kundipatsa chizindikiro choti mudzachitadi zimene mwalonjeza, kuti monga inu ndakuchitirani chifundo, inunso mudzachitira chifundo a pa banja la abambo anga. Inu mulonjeze kuti simudzapha abambo anga ndi amayi anga, abale anga ndi alongo anga ndi mabanja awo omwe.” Anthuwo anamuyankha kuti, “Ife ndife okonzeka kufa chifukwa cha inu. Ngati iwe sudzawulula zimene tachitazi, ndiye kuti ife tidzakukomera mtima ndi kusunga pangano lathu ndi iwe, Yehova akadzatipatsa dziko lino.” Popeza nyumba ya Rahabe inali pa linga la mzindawo, azondi aja anatulukira pa zenera. Rahabe anawatsitsa pansi ndi chingwe. Iye anawawuza kuti, “Pitani ku mapiri kuti okuthamangiraniwo asakupezeni. Mukabisale kumeneko masiku atatu mpaka iwo atabwerera, ndipo kenaka muzikapita kwanu.” Anthuwo anati kwa iye, “Lonjezo limene watichititsa ifeli tidzalisungadi tikadzalowa mʼdzikoli, iwe udzamangirire kansalu kofiira pa zenera limene unatitulutsira, ndi kusonkhanitsa abambo ako, amayi ako, abale ako ndi banja lako lonse mʼnyumba muno. Ngati wina aliyense adzatuluka mʼnyumbamo kuti azikayendayenda mu msewu, magazi ake adzakhala pamutu pake, ife sitidzapalamula kanthu. Koma wina aliyense wokhala mʼnyumba mwakomo akadzaphedwa, mlandu udzakhala wathu. Komanso iwe ukangowulula zimene ife tikuchitazi ndiye kuti ife sitidzasunga zimene talonjezazi.” Rahabe anayankha kuti, “Zikhale monga mwaneneramo.” Kenaka iye anawatulutsa ndipo iwowo anapita. Pambuyo pake Rahabe anamangirira kansalu kofiira pa zenera paja. Azondi aja anachoka napita ku mapiri ndipo anakhalako masiku atatu. Apa nʼkuti otumidwa ndi mfumu aja atawafunafuna ponseponse nʼkubwerera osawapeza. Pambuyo pake azondi awiri aja anayamba ulendo wobwerera kwawo. Anatsika ku mapiri kuja, nawoloka mtsinje mpaka anakafika kwa Yoswa mwana wa Nuni. Ndipo anamuwuza zonse zimene zinawachitikira. Iwo anati kwa Yoswa, “Ndithu, Yehova wapereka dziko lonse mʼmanja mwathu. Anthu onse kumeneko akuchita nafe mantha.” Aisraeli Awoloka Yorodani Yoswa ndi Aisraeli onse anadzuka mmamawa nanyamuka ku Sitimu kupita ku Yorodani. Iwo anagona kumeneko asanawoloke mtsinje wa Yorodaniwo. Patatha masiku atatu, atsogoleri anayendera misasa yonse, kulangiza anthu kuti, “Mukaona ansembe a Chilevi atanyamula Bokosi la Chipangano la Yehova Mulungu wanu, inu munyamuke pa malo ano ndi kumalitsatira. Potero mudzadziwa njira yoti mudzere, popeza simunayendepo njira ino nʼkale lomwe. Koma musaliyandikire. Pakati pa inu ndi bokosilo pakhale mtunda pafupifupi kilomita imodzi.” Yoswa anawuza anthu kuti, “Dzipatuleni tsono pakuti mawa Yehova adzachita zodabwitsa pakati panu.” Mmawa mwake Yoswa ananena kwa ansembe kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano muwoloke ndipo mukhale patsogolo pa anthu.” Motero iwo analinyamula ndi kupita patsogolo pawo. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Lero Ine ndidzayamba kukukweza pamaso pa Aisraeli onse kuti adziwe kuti ndili nawe monga ndinalili ndi Mose. Ansembe amene akunyamula Bokosi la Chipangano uwalamule kuti, ‘Mukafika ku mtsinje wa Yorodani mulowe mu mtsinjemo ndi kuyima mʼmphepete.’ ” Yoswa anati kwa Aisraeli, “Bwerani pano mudzamve mawu a Yehova Mulungu wanu. Umu ndi mmene mudzadziwira kuti Mulungu wamoyo ali pakati panu. Inu mukamadzapita patsogolo Iye adzathamangitsa Akanaani, Ahiti, Ahivi, Aperezi, Agirigasi, Aamori ndi Ayebusi. Pamenepo, Bokosi la Chipangano la Mbuye wa dziko lonse lapansi lidzawoloka mu Yorodani patsogolo panu. Musankhe amuna khumi ndi awiri kuchokera ku fuko lililonse la Israeli. Mapazi a ansembe onyamula Bokosi la Yehova, Mbuye wa dziko lapansi, akadzangoponda mu Yorodani, madzi ake onse ochokera ku mtunda adzaleka kuyenda ndipo adzayima ngati chipupa.” Tsono Aisraeli anachoka ku misasa yawo kukawoloka mtsinje wa Yorodani. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano ndiwo anatsogolera anthuwo. Nyengo imeneyi inali yokolola ndipo mtsinje wa Yorodani umakhala wodzaza. Komabe, ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anafika ku Yorodani, ndipo atangoponda mʼmadzimo, madzi ochokera ku mtunda anasiya kuyenda. Madzi a Yorodani ochokera ku mtunda anawunjikana pamodzi ngati khoma lalitali pa mtunda wautali ndithu ndi mzinda wa Adama chapafupi ndi mzinda wa Zaretani. Madzi othamangira ku nyanja ya Araba, ngakhalenso amene amachokera kuti Nyanja ya Mchere amathera pamenepo. Choncho anthu anawoloka tsidya lina moyangʼanana ndi Yeriko. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anali chiyimire powuma, pakati pa Yorodani pamene Aisraeli amawoloka mpaka gulu lonse linamaliza kuwoloka powuma. Anthu onse atatha kuwoloka Yorodani, Yehova anati kwa Yoswa, “Sankha amuna khumi ndi awiri, mmodzi pa fuko lililonse. Tsono uwalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iwiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodani, pamalo pamene ansembe anayimirirapo. Miyalayo muwoloke nayo ndi kudzayitula pamalo pamene mukagone usiku uno.’ ” Choncho Yoswa anayitana amuna khumi ndi awiri amene anawasankha aja kuchokera pakati pa Aisraeli, mmodzi pa fuko lililonse, ndipo anawawuza kuti, “Lowani pakati pa mtsinje wa Yorodani, patsogolo pa Bokosi la Yehova Mulungu wanu. Ndipo aliyense wa inu atenge mwala pa phewa lake, monga mwa chiwerengero cha mafuko a Aisraeli, kuti ikhale chizindikiro kwa inu. Mʼtsogolo muno ana anu akamadzakufunsani kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’ Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ” Aisraeli anachitadi monga Yoswa anawalamulira. Iwo ananyamula miyala khumi ndi iwiri kuchokera pakati pa Yorodani, fuko lililonse la Israeli mwala wake, monga Yehova analamulira Yoswa. Miyalayo anapita nayo ku misasa yawo nakayikhazika kumeneko. Yoswa anayimika miyala khumi ndi iwiri imene inali pakati pa Yorodani pamalo pamene ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anayimapo. Ndipo miyalayo ili pamalo pomwepo mpaka lero lino. Ansembe onyamula Bokosi lija anayimirirabe pakati pa Yorodani mpaka zonse zimene Yehova analamulira Yoswa kuti awuze anthu zinatha. Zimenezi zinali monga momwe Mose anamufotokozera Yoswa. Tsono anthu anawoloka mtsinjewo mofulumira. Anthu atatha kuwoloka, ansembe anatsogolera anthuwo atanyamula Bokosi la Yehova. Anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawoloka patsogolo pa Aisraeli ali ndi zida, monga momwe Mose anawalamulira. Asilikali pafupifupi 40,000 anawoloka napita kukayima mʼchigwa cha Yeriko kukonzekera nkhondo. Zimene Yehova anachita tsiku limeneli zinapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo anamulemekeza masiku onse a moyo wake, monga momwe analemekezera Mose. Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Lamula ansembe onyamula Bokosi la Chipanganowo kuti atuluke mu Yorodani.” Choncho Yoswa anawalamuladi ansembe aja kuti atuluke mu Yorodani muja. Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova aja atangotuluka mu mtsinje muja nʼkuponda powuma, madzi a mu Yorodani anayambanso kuyenda ngati poyamba mpaka kumasefukira. Aisraeli anawoloka Yorodani tsiku lakhumi la mwezi woyamba ndipo anakamanga misasa yawo ku Giligala mbali ya kummawa kwa Yeriko. Ku Giligala, Yoswa anayimikako miyala khumi ndi iwiri imene anayitenga mu Yorodani ija. Ndipo iye anati kwa Aisraeli, “Mʼtsogolo muno pamene adzukulu anu adzafunsa makolo awo kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’ Muzidzawawuza kuti, ‘Aisraeli anawoloka Yorodani pansi pali powuma.’ Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anawumitsa Yorodani pamaso panu mpaka inu mutawoloka. Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yorodani monga mmene anachitira ndi Nyanja Yofiira mpaka ife tinawoloka powuma. Iye anachita zimenezi kuti anthu onse pa dziko lapansi adziwe kuti dzanja la Yehova ndi lamphamvu, ndi kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.” Mwambo wa Mdulidwe pa Giligala Mafumu onse a Aamori, a kummawa kwa Yorodani ndi mafumu onse a Akanaani a mʼmbali mwa Nyanja anamva momwe Yehova anawumitsira Yorodani pamene Aisraeli ankawoloka. Choncho anachita mantha ndi kutayiratu mtima chifukwa cha Aisraeliwo. Tsono Yehova anati kwa Yoswa, “Panga mipeni ya miyala ndipo uchitenso mwambo wa mdulidwe pa Aisraeli.” Choncho Yoswa anapanga mipeni ya miyala ndi kuchita mdulidwe Aisraeli ku Gibeyati Haaraloti. Chifukwa chimene Yoswa anachitira izi ndi ichi: Onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto, amuna onse amene anali oyenera kumenya nkhondo anatha kufa mʼchipululu atatuluka mʼdziko la Igupto. Anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Igupto anali atachita mwambo wa mdulidwe, koma onse amene anabadwira mʼchipululu, pa ulendo wochoka ku Igupto, sanachite. Aisraeli anakhala akuyenda mʼchipululu kwa zaka makumi anayi mpaka amuna onse amene potuluka mʼdziko la Igupto anali a msinkhu woyenera kupita ku nkhondo anamwalira. Iwo anafa chifukwa sanamvere mawu a Yehova. Yehova anawalumbirira kuti sadzalowa konse mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi limene analonjeza kwa makolo awo kuti adzatipatsa. Koma ana awo amene analowa mʼmalo mwawo ndiwo amene Yoswa anawachita mdulidwe popeza sanachite pamene anali pa ulendo wawo mʼchipululu muja. Atamaliza kuchita mdulidwe uja, anthu onse anakakhala ku misasa yawo kudikira kuti zilonda zipole. Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Kuyambira tsopano anthu a ku Igupto sadzakunyozaninso.” Nʼchifukwa chake malowa anatchedwa Giligala mpaka lero. Akupumulabe ku Giligala kuja mʼchigwa cha Yeriko, Aisraeli anachita chikondwerero cha Paska madzulo pa tsiku la 14 la mwezi woyamba womwewo. Mmawa mwake ndi pamene anayamba kudya zakudya za mʼdziko la Kanaani. Anaphika buledi wopanda yisiti ndi kukazinga tirigu tsiku lomwelo. Atangodya chakudya cha mʼdzikomo, mana anasiya kugwa, ndipo sanapezekenso. Kuyambira nthawi imeneyo Aisraeli anayamba kudya chakudya cha mʼdziko la Kanaani. Kugwa kwa Makoma a Yeriko Tsiku lina pamene Yoswa anali pafupi ndi Yeriko, anakweza maso ake ndipo mwadzidzidzi anaona munthu atayima patsogolo pake ndi lupanga losolola mʼdzanja lake. Yoswa anapita pamene panali munthuyo ndipo anamufunsa kuti, “Kodi uli mbali yathu kapena ya adani athu?” Iye anayankha kuti “Sindili mbali iliyonse. Ndabwera monga mkulu wa asilikali a Yehova.” Pomwepo Yoswa anadzigwetsa chafufumimba kupereka ulemu, ndipo anamufunsa, “Kodi mbuye wanga muli ndi uthenga wotani kwa mtumiki wanu?” Mkulu wa asilikali a Yehova uja anayankha kuti, “Vula nsapato zako, pakuti wayima pa malo wopatulika.” Ndipo Yoswa anachitadi zimene anawuzidwazo. Tsono mzinda wa Yeriko unali utatsekedwa kuti Aisraeli asalowe. Palibe amene amatuluka kapena kulowa. Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Taona ndapereka Yeriko, pamodzi ndi mfumu yake ndi ankhondo ake mʼmanja mwako. Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse muzizungulira mzindawu masiku asanu ndi limodzi, kamodzi pa tsiku. Ansembe asanu ndi awiri, atanyamula malipenga a nyanga za nkhosa zazimuna, akhale patsogolo pa Bokosi la Chipangano. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzazungulire mzindawu kasanu ndi kawiri ansembe akuliza malipenga. Ansembe adzalize malipenga kosalekeza. Tsono anthu onse akadzamva kuliza kumeneku adzafuwule kwambiri, ndipo makoma a mzindawo adzagwa. Zikadzatero ankhondo adzalowe mu mzindawo.” Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anayitana ansembe ndipo anawawuza kuti, “Nyamulani Bokosi la Chipangano cha Yehova ndipo ansembe asanu ndi awiri anyamule malipenga. Iwowa akhale patsogolo pake.” Ndipo analamulira anthu kuti, “Yambani kuyenda! Yendani mozungulira mzinda ndipo ankhondo akhale patsogolo pa Bokosi la Yehova.” Mofanana ndi mmene Yoswa anayankhulira kwa anthu aja, ansembe asanu ndi awiri anapita patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Yehova akuliza malipenga a nyanga za nkhosa zija, ndipo Bokosi la Chipangano cha Yehova limabwera pambuyo pawo. Ankhondo amayenda patsogolo pa ansembe amene amayimba malipenga, ndiponso gulu lina pambuyo pa Bokosilo. Nthawi yonseyi nʼkuti malipenga akulira. Koma Yoswa nʼkuti atalamulira anthu kuti, “Musafuwule, musakweze mawu anu kapena kuyankhula mpaka tsiku limene ndidzakuwuzani kuti mufuwule. Pamenepo mudzafuwule!” Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova anazungulira mzindawo kamodzi. Kenaka anthu anabwerera ku msasa wawo kukagona. Yoswa anadzuka mmawa tsiku linalo ndipo ansembe ananyamula Bokosi la Yehova. Ansembe asanu ndi awiri onyamula malipenga asanu ndi awiri anakhala patsogolo pa Bokosi la Yehova akuyimba malipenga. Ankhondo anali patsogolo pawo ndipo gulu lina linatsatira Bokosi la Yehova. Apa nʼkuti malipenga akulira. Tsiku lachiwiri anazunguliranso mzinda kamodzi ndi kubwerera ku misasa. Iwo anachita izi kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, anadzuka mʼbandakucha ndipo anazungulira mzindawo kasanu ndi kawiri. Ndi pa tsiku lokhali limene anazungulira mzindawu kasanu ndi kawiri. Pomwe amazungulira kachisanu ndi chiwiri, ansembe akuliza malipenga mokweza, Yoswa analamulira anthu kuti “Fuwulani pakuti Yehova wakupatsani mzindawu! Mzindawu ndi zonse zimene zili mʼmenemo muziwononge. Rahabe yekha, mayi wadama, ndi aliyense amene ali pamodzi naye mʼnyumba mwake asaphedwe, chifukwa anabisa anthu odzazonda, amene ife tinawatuma Koma musatenge kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa. Mukadzangotenga kanthu kalikonse koyenera kuwonongedwa, mudzaputa mavuto, misasa ya Israeli idzawonongedwa. Zonse za siliva ndi golide, ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo, ndi zake za Yehova ndipo ziyenera kukasungidwa mosungiramo chuma chake.” Ansembe analiza malipenga. Anthu atamva kulira kwa malipenga, anafuwula kwambiri ndipo makoma a Yeriko anagwa. Choncho ankhondo anabwera ku mzinda uja nawulanda. Iwo analowa mu mzindawo nawononga ndi lupanga chilichonse chamoyo kuyambira amuna, akazi, ana ndi akulu, ngʼombe, nkhosa ndi abulu. Yoswa anawuza anthu awiri amene anakazonda dziko aja kuti, “Pitani ku nyumba ya mkazi wadama uja ndipo mukamutulutse iye pamodzi ndi onse amene ali naye ndipo mukabwere nawo kuno, munamulumbirira.” Choncho iwo anapita nakatenga Rahabe, abambo ake ndi amayi ake, abale ake ndi onse amene anali naye. Iwo anatulutsa banja lake lonse ndipo analiyika kuseri kwa msasa wa Aisraeli. Kenaka iwo anawotcha mzinda wonse ndi chilichonse chimene chinali mʼmenemo, kupatulapo zasiliva ndi zagolide pamodzi ndi ziwiya zamkuwa ndi zachitsulo zimene anakaziyika mʼnyumba yosungiramo chuma cha Yehova. Koma Yoswa sanaphe Rahabe, mkazi wadamayo pamodzi ndi banja lake ndi onse amene anali naye, chifukwa anabisa anthu amene iye anawatuma kukazonda Yeriko. Zidzukulu zake za Rahabeyo zikukhala pakati pa Aisraeli mpaka lero. Pa nthawi imeneyo Yoswa anapereka chenjezo motemberera kuti, “Akhale wotembereredwa pamaso pa Yehova munthu amene adzamangenso mzinda uwu wa Yeriko: “Aliyense amene adzayike maziko ake, mwana wake wamwamuna wachisamba adzafa, aliyense womanga zipata zake mwana wake wamngʼono adzafa.” Motero Yehova anali ndi Yoswa, ndipo mbiri yake inafalikira dziko lonse. Tchimo la Akani Koma Aisraeli anachita zachinyengo ndi lamulo lija loti asatenge kalikonse koyenera kuwonongedwa. Akani mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera, wa fuko la Yuda anatengako zinthu zina. Choncho Yehova anakwiyira Israeli kwambiri. Tsono Yoswa anatuma anthu kuchokera ku Yeriko kukazonda ku mzinda wa Ai umene uli pafupi ndi mzinda wa Beti-Aveni kummawa kwa Beteli, ndipo anawawuza kuti, “Pitani mukazonde chigawochi.” Anthuwo anapitadi kukazonda Ai. Atabwera kwa Yoswa, anamuwuza kuti, “Sikofunika kuti apite anthu onse kukathira nkhondo mzinda wa Ai. Mutumizeko anthu 2,000 kapena 3,000 kuti akatenge mzindawo. Musawatume anthu onse kumeneko popeza kuli anthu ochepa.” Choncho kunapita anthu 3,000. Koma iwo anathamangitsidwa ndi anthu a ku Ai. Anthu a ku Ai anathamangitsa Aisraeli kuchokera pa chipata cha mzindawo mpaka ku ngwenya ndipo anapha anthu 36. Iwowa anawapha pamene ankatsika phiri. Choncho mitima ya anthu inasweka ndipo analibenso mphamvu. Tsono Yoswa anangʼamba zovala zake nagwada nʼkuweramitsa mutu wake pansi patsogolo pa Bokosi la Yehova. Akuluakulu a Israeli nawonso anadzigwetsa pansi ndipo anakhala pomwepo mpaka madzulo atadziwaza fumbi kumutu kwawo. Ndipo Yoswa anati, “Kalanga ine, Ambuye Wamphamvuzonse chifukwa chiyani munatiwolotsa Yorodani? Kodi mumalinga zotipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge chotere? Kukanakhala kwabwino ife tikanakhala tsidya linalo la Yorodani! Tsono Ambuye, ine ndinene chiyani, pakuti tsopano Israeli anathamangitsidwa ndi adani ake? Akanaani ndi anthu ena a dziko lino adzamva zimenezi ndipo adzatizinga ndi kutiwonongeratu. Nanga inu mudzatani ndi dzina lanu lamphamvulo?” Koma Yehova anati kwa Yoswa, “Imirira! Chifukwa chiyani wagwada pansi chotere? Aisraeli achimwa. Iwo aphwanya pangano limene ndinawalamula kuti asunge. Anatengako zinthu zina zofunika kuwonongedwa. Choncho anabako, ananena bodza ndi kuyika zinthu zakubazo pamodzi ndi katundu wawo. Nʼchifukwa chake Aisraeli sangathe kulimbana ndi adani awo. Iwo anathawa pamaso pa adani awo chifukwa ndiwo oyenera kuwonongedwa. Ine sindikhalanso ndi inu pokhapokha mutawononga chilichonse choyenera kuwonongedwa pakati panu. “Nyamuka, ukawawuze anthu kuti, ‘Mudzipatule nokha kukonzekera kuonana nane mawa; pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti choyenera kuwonongedwa chija chili pakati panu, inu Aisraeli. Simungathe kulimbana ndi adani anu mpaka mutachichotsa.’ “Mawa mmamawa adzabwere pamaso pa Yehova fuko limodzilimodzi. Fuko limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo mbumba imodziimodzi. Tsono mbumba imene Yehova adzayiloze idzabwere patsogolo banja limodzilimodzi. Banja limene Yehova adzaliloze lidzabwere patsogolo munthu mmodzimmodzi. Iye amene adzagwidwe ndi zinthu zoyenera kuwonongedwazo adzawotchedwa ndi moto, pamodzi ndi banja lake lonse ndi zinthu zake zonse. Iyeyutu wachita chinthu chonyansa pakati pa Aisraeli ndi kuphwanya pangano limene anthu anga anachita ndi Ine!” Mmawa mwake Yoswa anabweretsa Israeli fuko limodzilimodzi ndipo fuko la Yuda linalozedwa. Anabweretsa poyera mbumba zonse za fuko la Yuda, ndipo mbumba ya Zera inagwidwa. Kenaka anatulutsa poyera mabanja onse a mbumba ya Zera ndipo banja la Zabidi linagwidwa. Potsiriza anatulutsa anthu onse a banja la Zabidi ndipo Akani anagwidwa. Iyeyu anali mwana wa Karimi, mwana wa Zabidi, mwana wa Zera wa fuko la Yuda. Ndipo Yoswa anati kwa Akani, “Mwana wanga pereka ulemerero kwa Yehova Mulungu wa Israeli ndipo umuyamike Iye. Ndiwuze zimene wachita, ndipo usandibisire.” Akani anayankha kuti, “Zoona! Ine ndachimwira Yehova Mulungu wa Israeli. Chimene ndachita ine ndi ichi: Ndinaona mwa zinthu zolanda ku nkhondo zija, mkanjo wokongola wa ku Babuloni, makilogalamu awiri a siliva ndiponso golide wolemera theka la kilogalamu. Zimenezi ndinazikhumba ndipo ndinazitenga. Ndazibisa mʼkati mwa tenti yanga, ndipo siliva ali pansi pake.” Motero Yoswa anatuma anthu, ndipo anathamanga kupita ku tenti. Anthuwo anakapeza kuti zinthuzo zinabisidwadi mʼtenti yake, ndipo siliva analidi pansi pake. Iwo anazichotsa zinthuzo mu tenti yake nabwera nazo kwa Yoswa ndi kwa Aisraeli onse ndipo anaziyika pamaso pa Yehova. Kenaka Yoswa pamodzi ndi Aisraeli onse anatenga Akani mwana wa Zera pamodzi ndi siliva, mkanjo, golide zimene anapezeka nazo zija. Anatenganso ana ake aamuna ndi aakazi, ngʼombe zake, abulu ndi nkhosa, tenti yake ndi zonse anali nazo, kupita nazo ku chigwa cha Akori. Yoswa anati “Chifukwa chiyani wabweretsa mavuto awa pa ife? Yehova ndiye abweretse mavuto pa iwe lero.” Kenaka Aisraeli onse anaponya miyala Akani, namupha. Anaponyanso miyala banja lake lonse, nʼkulipha. Pambuyo pake anatentha Akani uja, banja lake ndi zonse zimene anali nazo. Anawunjika mulu waukulu wa miyala pa Akani, imene ilipobe mpaka lero. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa chigwa cha Akori mpaka lero. Ndipo Yehova anachotsa mkwiyo wake. Kuwonongedwa kwa Mzinda wa Ai Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, “Usachite mantha kapena kutaya mtima. Tenga gulu lonse la nkhondo, ndipo upite ku Ai. Taona, ndapereka mfumu ya Ai pamodzi ndi anthu ake, mzinda wake ndi dziko lake lonse mʼmanja mwako. Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.” Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo. Ine ndi gulu langa lonse tikayamba kuwuputa mzindawu, ndipo akadzangotuluka kudzalimbana nafe, ife tidzawathawa monga tinachitira poyamba. Iwo adzatithamangitsa mpaka titawakokera kutali ndi mzindawo, pakuti iwo adzati, ‘Akutithawa monga anachitira poyamba.’ Pamene ife tizidzathawa, inu mudzatuluke pamene mwabisalapo ndi kulanda mzindawo. Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mzindawo. Mukakawulanda mzindawo mudzawuyatse moto. Mukachite monga mwa mawu a Yehova. Amenewa ndiwo malamulo amene ndakupatsani.” Yoswa atawatumiza, anapita ku malo wokabisalakowo ndipo anadikirira kumeneko. Malowa anali pakati pa Beteli ndi Ai, kumadzulo kwa Ai. Koma Yoswa anagona usiku umenewu pakati pa gulu lake lankhondo. Mmawa mwake, Yoswa anadzuka nayitana asilikali ake. Tsono iye pamodzi ndi akuluakulu a Aisraeli anatsogola kupita ku Ai. Gulu lonse la nkhondo limene linali ndi iye linatsogolako ndi kukamanga zithando pafupi ndi mzindawo chakumpoto mopenyana nawo. Pakati pa iwo ndi mzindawo panali chigwa. Yoswa anali atatenga asilikali 5,000 ndi kuwabisa pakati pa Ai ndi Beteli, kumadzulo kwa mzindawo. Anakhazika anthuwo mokonzekera nkhondo. Gulu lalikulu la nkhondo linakamanga zithando zawo kumpoto kwa mzinda, ndipo gulu lina linakamanga zithando zawo kumadzulo kwa mzindawo. Usiku umenewo Yoswa anakagona ku chigwa. Mfumu ya Ai itaona ankhondo a Yoswa, inachita zinthu mofulumira. Inadzuka mmamawa ndipo inapita pamodzi ndi anthu ake ku malo otsika oyangʼanana ndi Araba kuti akachite nkhondo ndi Aisraeli. Koma iyo sinadziwe kuti ayithira nkhondo kudzera kumbuyo kwa mzindawo. Yoswa ndi Aisraeli onse anachita ngati agonja ndi kumathawira ku chipululu. Anthu onse a ku Ai anawuzidwa kuti awapirikitse. Ndipo iwo anapirikitsadi Yoswa uja, ndi kupita kutali ndi mzinda wawo. Palibe munthu wamwamuna wa mzinda wa Ai kapena wa Beteli amene sanatuluke kukapirikitsa Aisraeli. Iwo anasiya mzinda wosatseka ndi kumapirikitsa Aisraeli. Ndipo Yehova anati kwa Yoswa, “Loza mkondo uli mʼdzanja lako ku Ai pakuti ine ndipereka mʼdzanja lanu mzindawo.” Kotero Yoswa analoza mkondowo ku Ai. Atangotambalitsa dzanja lake, anthu amene anabisala aja ananyamuka msangamsanga pamalo pawo ndi kuthamangira kutsogolo. Iwo analowa mu mzindamo ndi kuwulanda ndipo anawutentha mofulumira. Anthu a ku Ai aja atangochewukira mʼmbuyo anaona utsi uli tolotolo. Koma mpata woti athawireko panalibe pakuti Aisraeli amene amathawira ku chipululu anabwerera nayamba kuwathamangitsa. Yoswa ndi Aisraeli onse ataona kuti obisalira aja alanda mzinda ndipo kuti utsi unali tolotolo, iwo anatembenuka ndi kuyamba kupha anthu a ku Ai. Nawonso Aisraeli amene anali mu mzindamo anatuluka kudzalimbana ndi anthu a ku Ai. Choncho iwo anazingidwa mbali zonse ndi Aisraeli ndipo onse anaphedwa. Palibe amene anatsala wamoyo kapena wothawa kupatula mfumu ya ku Ai yokha imene anayigwira nabwera nayo kwa Yoswa. Aisraeli aja atatha kupha anthu onse a ku Ai amene anali mʼthengo ndi mʼchipululu kumene anawapirikitsira, onse anabwerera ku Ai ndi kupha onse amene anali mu mzindamo. Chiwerengero cha anthu onse a ku Ai, amuna ndi akazi, amene anaphedwa pa tsiku limeneli chinali 12,000. Yoswa sanatsitse dzanja lake limene ananyamula mkondo mpaka ataona kuti onse amene amakhala mu mzinda wa Ai aphedwa. Tsono Aisraeli anatenga zoweta ndi katundu yense wa anthu ophedwa aja, monga momwe Yehova analamulira Yoswa. Pambuyo pake Yoswa anawutentha mzinda wa Ai ndi kuwusiya bwinja monga ulili leromu. Iye anapachika pa mtengo mfumu ya Ai ndipo anayisiya mpaka madzulo. Pomwe dzuwa linalowa Yoswa analamula kuti akachotse mtembowo ndi kukawutaya ku chipata cha mzindawo. Pamwamba pa mtembowo anawunjikapo mulu waukulu wa miyala. Muluwo ulipobe mpaka lero lino. Kuchitanso Pangano pa Phiri la Ebala Ndipo Yoswa anamanga guwa lansembe la Yehova Mulungu wa Israeli pa phiri la Ebala. Analimanga motsata zimene Mose mtumiki wa Yehova analamulira Aisraeli, ndiponso potsata zomwe zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose kuti guwa lansembe likhale la miyala yosasemedwa ndi chitsulo. Pa guwalo anapereka kwa Yehova nsembe yopsereza ndi nsembe yachiyanjano. Kenaka anthu onse akupenya, Yoswa analemba pa miyala chitsanzo cha malamulo amene Mose analemba. Aisraeli onse, akuluakulu awo, atsogoleri awo ndi oweruza awo, alendo pamodzi ndi mbadwa, anayimirira mbali zonse ziwiri za Bokosi la Chipangano la Yehova, ena uku ena uku moyangʼanana ndi ansembe a Chilevi. Theka la anthu linayima patsogolo pa phiri la Gerizimu ndipo theka lina patsogolo pa phiri la Ebala, monga momwe Mose mtumiki wa Yehova anawalamulira mʼmbuyomo pamene anawapatsa malangizo podalitsa Aisraeli. Pambuyo pake Yoswa anawerenga mawu onse a malamulo, madalitso ndi matemberero monga momwe zinalembedwera mʼbuku la malamulo a Mose. Yoswa anawerenga mawu onse amene Mose analamula, gulu lonse la Israeli limene linasonkhana likumva. Amayi, ana ndi alendo omwe okhala pakati pawo anali pomwepo. Chinyengo cha Agibiyoni Mafumu onse okhala kumadzulo kwa Yorodani atamva zimenezi pamodzi ndi mafumu okhala ku mayiko a ku mapiri, mu zigwa, mʼmbali mwa Nyanja yayikulu mpaka ku Lebanoni (mafumu a Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi), anapangana kuti achite nkhondo ndi Yoswa ndi Israeli. Koma Ahivi ena a ku Gibiyoni atamva zomwe Yoswa anachitira mizinda ya Yeriko ndi Ai, anaganiza zochita zachinyengo. Anapita nasenzetsa abulu awo chakudya mʼmatumba akalekale ndiponso matumba a vinyo achikopa ongʼambikangʼambika. Anthuwa anavala nsapato zakutha ndi zazigamba ndiponso anavala sanza. Buledi wawo yense anali wowuma ndi wowola. Ndipo anapita kwa Yoswa ku msasa ku Giligala ndikumuwuza kuti, pamodzi ndi Aisraeli onse, “Ife tachokera ku dziko lakutali, ndipo tikufuna kuti muchite mgwirizano ndi ife.” Koma Aisraeli anayankha Ahiviwo kuti, “Mwinatu inu mukukhala pafupi ndi ife. Tsono ife tingachite bwanji mgwirizano ndi inu?” Iwo anati kwa Yoswa, “Ife ndife akapolo anu.” Tsono Yoswa anawafunsa kuti, “Inu ndinu yani ndipo mukuchokera kuti?” Iwo anayankha kuti, “Akapolo anufe tachokera ku dziko lakutali chifukwa tamva za Yehova Mulungu wanu. Tamva mbiri yonse ya zimene Iye anachita ku Igupto, ndi zonse zimene anachita kwa mafumu awiri a Aamori kummawa kwa Yorodani, mfumu Sihoni ya Hesiboni ndi Ogi mfumu ya Basani amene amalamulira ku Asiteroti. Tsono akuluakulu athu ndi onse amene akukhala mʼdziko lathu anati kwa ife. Tengani chakudya cha pa ulendo wanu. Pitani mukakumane nawo ndipo mukati kwa iwo, ‘Ife ndife akapolo anu, ndipo tikufuna kuti mugwirizane nafe za mtendere.’ ” Buledi wathuyu anali wotentha pamene timanyamuka ku mudzi kubwera kwa inu. Koma tsopano taonani ali gwaa ndiponso wawola. Zikopa zimene tinathiramo vinyozi zinali zatsopano, koma taonani zathetheka. Zovala zathu ndi nsapato zathu zatha chifukwa cha kutalika kwa ulendo. Aisraeli anatengako chakudya chawo koma sanafunse kwa Yehova. Choncho Yoswa anapangana nawo za mtendere kuti sadzawapha, ndipo atsogoleri a gulu anavomereza pochita lumbiro. Patatha masiku atatu atachita mgwirizano wa mtendere ndi Agibiyoni, Aisraeli anamva kuti anali anansi awo, anthu amene amakhala nawo pafupi. Tsono Aisraeli ananyamuka ulendo ndipo tsiku lachitatu anafika ku mizinda ya Gibiyoni, Kefira, Beeroti ndi Kiriati-Yearimu. Koma Aisraeli sanawaphe anthuwo chifukwa atsogoleri awo anali atalonjeza mʼdzina la Yehova Mulungu wa Israeli za Agibiyoniwo. Koma anthu onse anatsutsana ndi atsogoleriwo. Koma atsogoleriwo anayankha kuti, “Ife tinawalonjeza mʼdzina la Yehova, Mulungu wa Israeli, ndipo tsopano sitingawaphe. Chimene tidzachita nawo ndi ichi: Tidzawasiya akhale ndi moyo kuti mkwiyo wa Yehova usatigwere chifukwa chophwanya lonjezo limene tinawalonjeza.” Anapitiriza kunena kuti “Asiyeni akhale ndi moyo, komabe akhale otidulira mitengo ndi kutitungira madzi ogwiritsa ntchito pa chipembedzo.” Lonjezo la atsogoleriwo linasungidwa. Kenaka Yoswa anayitanitsa Agibiyoni aja nawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani inu munatinyenga ponena kuti mumachokera kutali pamene zoona zake nʼzoti mumakhala pafupi pomwe pano? Tsopano popeza mwachita izi, Mulungu wakutembererani ndipo palibe wina mwa inu amene akhale mfulu. Nthawi zonse inu muzidzatidulira nkhuni ndi kutitungira madzi ku Nyumba ya Yehova.” Iwo anayankha Yoswa kuti, “Ife akapolo anufe tinachita zimenezi chifukwa tinamva bwino lomwe kuti Yehova Mulungu wanu analamula Mose mtumiki wake kuti adzakupatsani dziko lonseli ndi kuti anthu onse okhalamo adzaphedwe. Tsono ife tinachita mantha aakulu ndipo tinachita zimenezi pofuna kupulumutsa miyoyo yathu. Tsopanotu ife tili mʼmanja mwanu, ndipo inu chitani nafe monga kukukomerani.” Tsono Yoswa anawapulumutsa mʼmanja mwa Aisraeli ndipo sanawaphe. Kuyambira tsiku limenelo Agibiyoni aja anasanduka odula nkhuni zaguwa lansembe la Yehova ndiponso otunga madzi. Mpaka lero lino iwo akuchitabe zimenezi kulikonse kumene Yehova anasankha. Kuyimitsidwa kwa Dzuwa Adoni-Zedeki mfumu ya ku Yerusalemu inamva kuti Yoswa wagonjetsa ndi kuwononga kotheratu mzinda wa Ai pamodzi ndi mfumu yake, monga anachitira ndi Yeriko ndi mfumu yake. Inamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni anachita pangano la mtendere ndi Israeli ndipo amakhala pakati pawo. Choncho iye ndi anthu ake anachita mantha aakulu, chifukwa Gibiyoni unali mzinda waukulu kwambiri, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu ndipo ankhondo ake anali olimba mtima. Chotsatira chake Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu inatuma uthenga kwa Hohamu mfumu ya Hebroni, Piramu mfumu ya Yarimuti, Yafiya mfumu ya Lakisi ndi Debri mfumu ya Egiloni. Iye anatumiza mawu kuti, “Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake achita pangano la mtendere ndi Yoswa ndi Aisraeli.” Mafumu asanu a Aamori aja, mfumu ya Yerusalemu, mfumu ya Hebroni, mfumu ya Yarimuti, mfumu ya Lakisi ndi mfumu ya Egiloni, anagwirizana. Iwo anasonkhanitsa ankhondo awo nazungulira mzinda wa Gibiyoni ndi kuwuthira nkhondo. Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.” Choncho Yoswa ananyamuka kuchoka ku Giligala ndi gulu lake la ankhondo pamodzi ndi anthu ake olimba mtima. Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope, Ine ndawapereka mʼdzanja lako. Palibe ndi mmodzi mwa amenewa amene adzalimbe.” Atayenda usiku wonse kuchokera ku Giligala, Yoswa anawathira nkhondo mwadzidzidzi. Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda. Pamene ankathawa pamaso pa Israeli pa njira yochokera ku Beti-Horoni mpaka ku Azeka, Yehova anawagwetsera matalala akuluakulu kuchokera kumwamba ndipo ambiri mwa iwo anafa ndi matalala kuposa amene anaphedwa ndi lupanga la Israeli. Pa tsiku limene Yehova anapereka Aamori mʼmanja mwa Israeli, Yoswa ananena kwa Yehova pamaso pa Israeli kuti, “Iwe dzuwa, ima pamwamba pa Gibiyoni, mwezi ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.” Choncho dzuwa linayima, mwezinso unayima, mpaka dziko la Israeli litagonjetsa adani ake. Zimenezi zalembedwa mʼbuku la Yasari. Dzuwa linayima pamodzimodzi pakati pa thambo mlengalenga, osayendanso kwa tsiku lathunthu. Sipanakhaleponso tsiku ngati limeneli kuyambira kale, tsiku limene Yehova anamvera munthu. Izi zinatero chifukwa Yehova ankamenyera nkhondo Aisraeli. Kenaka Yoswa anabwerera pamodzi ndi Aisraeli onse ku misasa ku Giligala. Kuphedwa kwa Mafumu Asanu a Aamori Mafumu asanu aja anathawa ndi kukabisala ku phanga la Makeda. Koma Yoswa anamva kuti mafumu asanu awapeza akubisala ku phanga la Makeda. Tsono Yoswa analamula kuti, “Mugubuduzire miyala ikuluikulu pa khomo la phangalo, ndipo muyike anthu ena kuti azilondera. Koma inu musakhaleko! Thamangitsani adani anu, muwathire nkhondo kuchokera kumbuyo ndipo musawalole kuti akafike ku mizinda yawo, pakuti Yehova Mulungu wanu wawapereka mʼmanja mwanu.” Kotero Yoswa ndi Aisraeli anapha anthu aja, kupatulapo ochepa amene anathawa nakabisala ku mizinda yawo. Kenaka gulu lonse la ankhondo linabwerera bwinobwino kwa Yoswa ku misasa ya ku Makeda, palibe aliyense mu mzindamo amene anaputanso Aisraeli. Yoswa anati, “Tsekulani khomo la phangalo ndipo muwabweretse kwa ine mafumu asanuwo.” Pamenepo mafumu asanu aja anatulutsidwa, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yarimuti, mfumu ya ku Lakisi, ndi mfumu ya ku Egiloni. Atabwera nawo kwa Yoswa, iye anayitana Aisraeli onse. Ndipo analamula akuluakulu ake amene anapita naye limodzi kuti, “Bwerani kuno ndipo apondeni pakhosi mafumuwa.” Yoswa anawawuza kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Khalani amphamvu ndi olimba mtima popeza umo ndi mmene Yehova adzachitire ndi adani anu onse amene mudzamenyana nawo.” Kenaka Yoswa anawabaya ndi kuwapha mafumuwo ndipo anawapachika pa mitengo isanu ndipo anakhala pamenepo mpaka madzulo. Dzuwa litalowa, Yoswa analamula kuti awachotse pa mitengo ija ndi kuwaponya mʼphanga limene ankabisalamo. Pa khomo pa phangalo anayikapo miyala ikuluikulu imene ilipo mpaka lero. Tsiku lomwelo Yoswa analanda mzinda wa Makeda. Iye anapha anthu a mu mzindamo ndi mfumu yake ndipo sanasiye aliyense wamoyo. Yoswa anachita ndi mfumu ya ku Makeda monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko. Agonjetsa Mizinda ya Kummwera Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Makeda nakafika ku Libina ndi kuthira nkhondo mzindawo. Yehova anaperekanso mzindawo ndi mfumu yake mʼmanja mwa Aisraeli. Ndipo Yoswa anapha onse amene anali mu mzindamo. Palibe amene anatsala wamoyo. Ndipo Yoswa anachita ndi mfumu ya Libina monga anachitira ndi mfumu ya Yeriko. Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Libina kupita ku Lakisi. Iye anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo. Yehova anapereka Lakisi kwa Israeli; ndipo Yoswa anawulanda pa tsiku lachiwiri. Monga anachita ndi mzinda wa Libina, Yoswa anapha anthu onse okhala mu mzinda wa Lakisi, ndipo palibe amene anatsala ndi moyo. Nthawi imeneyi nʼkuti Horamu mfumu ya Gezeri itabwera kudzathandiza Lakisi koma Yoswa anamugonjetsa pamodzi ndi asilikali ake ndipo palibe anatsala wamoyo. Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anapitirira kuchokera ku Lakisi nakafika ku Egiloni. Iwo anazungulira mzindawo ndi kuwuthira nkhondo. Anawulanda tsiku lomwelo ndipo anapha aliyense amene anali mu mzindawo monga momwe anachitira ku Lakisi. Kenaka Yoswa ndi Aisraeli onse anachoka ku Egiloni nakafika ku Hebroni ndi kukawuthira nkhondo. Iwo analanda mzindawo napha ndi lupanga mfumu yake pamodzi ndi onse amene ankakhala mʼmenemo. Monga anachita ndi mzinda wa Egiloni, kuti sanasiye aliyense ndi moyo, anachitanso chimodzimodzi ndi mzinda wa Hebroni. Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anatembenukira mzinda wa Debri ndi kukawuthira nkhondo. Iwo analanda mzindawo ndi midzi ndi kupha mfumu yake pamodzi ndi onse okhala mʼmenemo. Anachita ndi mzinda wa Debri pamodzi ndi mfumu yake zofanana ndi zimene anachita ndi mzinda wa Libina ndi wa Hebroni. Motero Yoswa anagonjetsa dziko lonselo. Anapha mafumu onse a dera la kumapiri, dera la kummawa, dera la kumadzulo mʼmphepete mwa phiri, ndiponso dera la ku magomo, kummwera. Iye sanasiye wina aliyense wamoyo. Anapha onse amene anali moyo monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli analamulira. Yoswa anawagonjetsa iwo kuyambira ku Kadesi Barinea mpaka ku Gaza, ndiponso kuchokera ku chigawo chonse cha Goseni mpaka ku Gibiyoni. Yoswa anagonjetsa mafumu onsewa ndi kulanda dziko lawo kamodzinʼkamodzi chifukwa Yehova Mulungu wa Israeli anawamenyera nkhondo. Pambuyo pake Yoswa ndi Aisraeli onse anabwerera ku misasa yawo ku Giligala. Kugonjetsedwa kwa Mafumu a Kumpoto Yabini, mfumu ya Hazori, inamva zimene zinachitikazi. Tsono inatumiza uthenga kwa Yobabu mfumu ya Madoni, ndiponso kwa mafumu a ku Simironi ndi Akisafu. Inatumizanso uthenga kwa mafumu a kumpoto, kumapiri, ndi mʼchigwa cha Yorodani kummwera kwa nyanja ya Kinereti, ndiponso kumadzulo mʼmbali mwa nyanja pafupi ndi Dori. Inatumizanso uthenga kwa Akanaani amene ankakhala kummawa ndi kumadzulo kwa Yorodani. Uthenga unapitanso kwa Aamori, Ahiti, Aperezi ndi Ayebusi amene amakhala mʼdziko la ku mapiri ndiponso kwa Ahivi amene ankakhala mʼmunsi mwa phiri la Herimoni ku chigwa cha Mizipa. Mafumuwo anabwera pamodzi ndi ankhondo awo onse. Gulu la ankhondo linali lalikulu ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Analinso ndi akavalo ndi magaleta ambiri. Mafumu onsewa anasonkhana pamodzi ndipo anamanga misasa yawo ku mtsinje wa Meromu, kuti amenyane ndi Israeli. Yehova anati kwa Yoswa, “Usawaope chifukwa mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzawapereka kuti muwaphe. Akavalo awo muwadule matsinde ndipo magaleta awo muwatenthe ndi moto.” Kotero Yoswa pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo anafika kwa adani awo aja ku mtsinje wa Meromu modzidzimutsa ndi kuwathira nkhondo. Yehova anawapereka mʼmanja mwa Israeli mwakuti anawagonjetseratu ndi kuwapirikitsa njira yonse mpaka ku Sidoni Wamkulu ndi ku Misirefoti Maimu, ndiponso kummawa ku chigwa cha Mizipa. Onse anaphedwa popanda wopulumuka. Yoswa anawachita zimene Yehova analamula. Iye anadula matsinde a akavalo awo ndi kutentha magaleta awo. Pambuyo pake Yoswa anabwera nalanda mzinda wa Hazori ndi kupha mfumu yake. (Nthawi imeneyo mzinda wa Hazori unali wopambana mizinda ina yonse). Anapha aliyense wa mu mzindamo popanda wotsala wamoyo, ndipo mzinda wa Hazori anawutentha ndi moto. Yoswa analanda mizinda yonse ndi mafumu ake. Anthu onse anaphedwa ndi lupanga monga momwe analamulira Mose, mtumiki wa Yehova. Israeli sanatenthe mizinda yomangidwa pa zitunda, kupatula mzinda wa Hazori, umene Yoswa anawutentha. Aisraeli anatenga zinthu zonse za mʼmizindayi pamodzi ndi ziweto kuti zikhale zawo, koma anapha anthu onse ndi lupanga osasiyako ndi mmodzi yemwe wamoyo. Monga momwe Yehova analamulira mtumiki wake Mose, nayenso Mose analamulira Yoswa ndipo Yoswa anachita chilichonse chimene Yehova analamulira Mose. Kotero Yoswa analanda dziko lonse: dziko la ku mapiri, dera lonse la Negevi, chigawo chonse cha Goseni, ndi chigwa chake chonse, chigwa cha Yorodani, dziko lonse la lamapiri la Israeli pamodzi ndi chigwa chake chomwe. Dziko lolandidwalo linayambira ku phiri la Halaki limene linali ku Seiri mpaka ku Baala-Gadi mʼchigwa cha Lebanoni, kumunsi kwa phiri la Herimoni. Yoswa anagwira ndi kupha mafumu a dziko lonselo atachita nawo nkhondo kwa nthawi yayitali. Palibe ngakhale ndi mfumu imodzi yomwe imene inachita mgwirizano wa mtendere ndi Aisraeli kupatula Ahivi okhala ku Gibiyoni. Koma mizinda ina yonse anachita kuyigonjetsa pa nkhondo. Yehova anali atawumitsa mitima yawo kuti alimbane ndi Aisraeli kuti aphedwe popanda kuchitiridwa chifundo. Izi ndi zimene Yehova analamula Mose kuti zichitidwe. Pa nthawi imeneyi Yoswa anapita kukawononga Aanaki okhala mʼdziko lija la ku mapiri ku Hebroni, Debri, Anabu komanso madera onse a ku mapiri a Yuda ndi Israeli. Yoswa anawawononga onse pamodzi ndi mizinda yawo. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsalako mʼdziko lonse la Israeli; komabe ku Gaza, ku Gati ndi Asidodi kokha ndi kumene anatsalako pangʼono. Choncho Yoswa anagonjetsa dziko lonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Tsono Yoswa analipereka kwa Aisraeli kuti likhale lawo, fuko lililonse gawo lake. Anthu onse anapumula, osamenyanso nkhondo. Mayina a Mafumu Ogonjetsedwa Aisraeli anagonjetsa dziko lonse la kummawa kwa Yorodani, kuyambira ku chigwa cha Arinoni mpaka ku phiri la Herimoni pamodzi ndi dera lonse la kummawa kwa Araba. Iwo anatenga dzikoli kukhala lawo, ndipo mafumu a dzikoli anali awa: Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala mu Hesiboni. Iye analamulira kuyambira ku Aroeri mzinda umene uli mʼmphepete mwa mtsinje wa Arinoni, mpaka ku mtsinje wa Yaboki, umene uli mʼmalire mwa Aamori, kuphatikizanso theka la dziko la Giliyadi. Iye ankalamuliranso dera la chigwa cha Yorodani kuyambira ku Nyanja ya Kinereti, kummawa ndi kumatsika mpaka ku Beti-Yesimoti, mzinda umene unali kummawa kwa Nyanja ya Mchere ndi kutsikabe kummwera mpaka pa tsinde pa phiri la Pisiga. Ogi mfumu ya mzinda wa Basani, amene anali mmodzi mwa otsala mwa Arefaimu. Iye ankakhala ku Asiteroti ndi Ederi. Dera la ufumu wake linafika ku phiri la Herimoni, ku Saleka ndi dziko lonse la Basani mpaka ku malire ndi anthu a ku Gesuri Makati. Ufumu wake unaphatikizanso theka la Giliyadi mpaka ku malire a mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Mose mtumiki wa Yehova ndi Aisraeli anawagonjetsa ndipo anapereka dziko lawo kwa anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase kuti chikhale cholowa chawo. Yoswa ndi Aisraeli onse anagonjetsa mafumu onse okhala kumadzulo kwa mtsinje wa Yorodani kuyambira ku Baala-Gadi, ku chigwa cha Lebanoni mpaka ku phiri la Halaki, kumapita cha ku Seiri. Yoswa anagawira dzikolo mafuko a Israeli kuti likhale cholowa chawo. Dziko limeneli linali dera la ku mapiri, chigwa cha kumadzulo, chigwa cha Yorodani, ku matsitso a kummawa, ndi dziko la chipululu la kummwera. Amene ankakhala mʼdzikoli anali Ahiti, Aamori, Akanaani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Mafumu ake anali awa: mfumu ya Yeriko imodzi mfumu ya Ai (kufupi ndi Beteli imodzi mfumu ya Yerusalemu imodzi mfumu ya Hebroni imodzi mfumu ya Yarimuti imodzi mfumu ya Lakisi imodzi mfumu ya Egiloni imodzi mfumu ya Gezeri imodzi mfumu ya Debri imodzi mfumu ya Gederi imodzi mfumu ya Horima imodzi mfumu ya Aradi imodzi mfumu ya Libina imodzi mfumu ya Adulamu imodzi mfumu ya Makeda imodzi mfumu ya Beteli imodzi mfumu ya Tapuwa imodzi mfumu ya Heferi imodzi mfumu ya Afeki imodzi mfumu ya Lasaroni imodzi mfumu ya Madoni imodzi mfumu ya Hazori imodzi mfumu ya Simuroni Meroni imodzi mfumu ya Akisafu imodzi mfumu ya Taanaki imodzi mfumu ya Megido imodzi mfumu ya Kadesi imodzi mfumu ya Yokineamu ku Karimeli imodzi mfumu ya Dori ku Nafoti Dori imodzi mfumu ya Goyini ku Giligala imodzi mfumu ya Tiriza imodzi   mafumu onse pamodzi analipo 31.
Mayiko Otsala Oyenera Kulandidwa Yoswa atakalamba Yehova anamuwuza kuti, Iwe tsopano wakalamba kwambiri, koma dziko losalandidwa lilipobe lalikulu. “Madera amene atsala ndi awa: chigawo chonse cha Afilisti ndi Agesuri kuchokera ku mtsinje wa Sihori kummawa kwa Igupto mpaka kumpoto kwa dziko la Ekroni. Madera onse amawerengedwa kuti ndi a Akanaani ngakhale amalamulidwa ndi mafumu asanu a Afilisti a ku Gaza, Asidodi, Asikeloni, Gati, Ekroni ndi Agiti, komanso ku Avimu ku chigawo cha kumpoto. Dziko lina la Akanaani ndi Ameara limene lili mʼmanja mwa Asidoni mpaka ku Afeki, dziko limene linachitana malire ndi dziko la Aamori. Palinso dziko lonse la Gebala ndi Lebanoni cha kummawa kuyambira ku Baala-Gadi pa tsinde pa phiri la Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. “Palinso anthu okhala mʼchigawo cha ku mapiri kuchokera ku Lebanoni mpaka ku Misirefoti-Maimu, Ine ndidzawapirikitsa pamene Aisraeli azidzalowa. Tsono uwagawire Aisraeli dziko limeneli kuti likhale cholowa chawo monga momwe ndakulamulira. Tsopano ugawire dziko limeneli mafuko asanu ndi anayi ndiponso theka la fuko la Manase, kuti likhale cholowa chawo.” Kugawidwa kwa Dziko la Kummawa kwa Yorodani Anthu a fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi pamodzi ndi theka lina la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo chimene Mose mtumiki wa Yehova anawapatsa. Cholowa chawocho chinali kummawa kwa mtsinje wa Yorodani. Dziko lawolo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, ndiponso mzinda umene uli pakati pa chigwacho. Dzikolo linkaphatikizanso dera lonse lokwera kuyambira ku Medeba mpaka ku Diboni. Linkaphatikizanso mizinda yonse ya mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkalamulira mu Hesiboni, mpaka ku malire a Aamoni. Dzikoli linaphatikizanso Giliyadi, dziko la anthu a ku Gesuri ndi Maaka, phiri lonse la Herimoni ndi dziko lonse la Basani mpaka ku Saleka. Linaphatikizanso dziko la mfumu Ogi ya ku Basani imene imalamulira kuchokera ku Asiteroti ndi Ederi. Iye yekha ndiye anali mfumu ya Arefaimu amene anapulumuka. Mose anali atawagonjetsa anthu amenewa ndi kuwathamangitsira kutali. Koma Aisraeli sanathamangitse anthu a ku Gesuri ndi Maaka, kotero iwowa amakhalabe pakati pawo mpaka lero. Koma Mose sanapereke dziko kwa fuko la Alevi popeza zopereka zopatulika zimene anthu ankapereka kwa Yehova, Mulungu wa Israeli, ndizo zinali cholowa chawo monga Yehova anawalonjezera. Mose anapereka gawo lina la dziko kwa mabanja a fuko la Rubeni. Dziko lawo linayambira ku Aroeri mzinda umene uli pafupi ndi chigwa cha Arinoni, mʼmudzi wa pakati pa chigwa, ndiponso dera lonse lokwera mpaka ku Medeba. Dzikolo linaphatikizanso Hesiboni ndi mizinda yake yonse, komanso mizinda monga Diboni, Bamoti Baala, Beti-Baala-Meoni, Yahaza, Kedemoti, Mefaati. Kiriataimu, Sibima, Zereti-Sahari, pa phiri limene lili mʼchigwa, Beti-Peori, ku matsitso a Pisiga, ndiponso Beti-Yesimoti. Dzikolo linaphatikizanso mizinda yonse ya ku madera okwera ndiponso dziko lonse la mfumu Sihoni ya Aamori amene ankalamulira kuchokera ku Hesiboni. Mose anamugonjetsa iye pamodzi ndi mafumu a Amidiyani awa: Evi, Rekemu, Zuri, Huri ndi Reba, mafumu amene anagwirizana ndi Sihoni. Onsewa analamulira dzikolo ngati nduna za Sihoni. Kuwonjezera pa amene anaphedwa ndi nkhondo, Aisraeli anapha ndi lupanga Balaamu mwana wa Beori, amene amachita za matsenga. Malire a fuko la Rubeni anali mtsinje wa Yorodani. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake zinapatsidwa kwa mabanja a fuko la Rubeni kuti akhale cholowa chawo. Dera limene Mose anapereka kwa mabanja a fuko la Gadi ndi ili: Dziko la Yazeri, mizinda yonse ya mu Giliyadi ndiponso theka la dziko la Amori kukalekezera ku Aroeri, kufupi ndi Raba; ndiponso kuyambira ku Hesiboni mpaka ku Ramati-Mizipa, ndi Betonimu; ndiponso kuyambira ku Mahanaimu mpaka ku dziko la Debri. Mu chigwa cha Yorodani analandiramo Beti-Haramu, Beti-Nimira, Sukoti ndi Zafoni pamodzi ndi dziko lonse la mfumu Sihoni ya ku Hesiboni. Malire ake a ku madzulo anali mtsinje wa Yorodani kufikira ku Nyanja ya Kinereti, kumpoto. Mizinda ndi midzi imeneyi inali cholowa cha mabanja a fuko la Gadi. Mose anali atapereka kale gawo lina la dziko limeneli kwa theka la mabanja a fuko la Manase kuti likhale cholowa chawo. Derali linayambira ku Mahanaimu kuphatikizapo dziko lonse la mfumu Ogi, Mfumu ya ku Basani, pamodzi ndi mizinda 60 ya ku Yairi, ku Basaniko. Derali linaphatikizanso theka la Giliyadi pamodzi ndi Asiteroti ndi Ederi, mizinda yayikulu ya mfumu Ogi wa Basani. Mizinda imeneyi inapatsidwa kwa mabanja a Makiri, mwana wa Manase kuti ikhale cholowa cha theka la ana a Makiri, malinga ndi mabanja awo. Umu ndi mmene Mose anagawira malo a mʼchigwa cha Yorodani, kummawa kwa Yeriko, ku tsidya kwa Yorodani. Komatu Mose sanapereke malo kwa fuko la Levi. Mose anawawuza kuti zopereka zimene anthu ankapereka kwa Yehova ndizo cholowa chawo. Kugawa kwa Dziko la Kumadzulo kwa Yorodani Umu ndi mmene Aisraeli analandirira cholowa chawo mʼdziko la Kanaani. Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni pamodzi ndi akuluakulu a mafuko a Israeli ndiwo anagawa dzikolo kugawira Aisraeli. Madera anagawidwa mwa maere kwa mafuko asanu ndi anayi ndi theka, monga momwe Yehova analamulira kudzera mwa Mose. Mose anapereka kwa mafuko awiri ndi theka dziko la kummawa kwa Yorodani, koma fuko la Levi lokha silinagawiridwe malo. Tsono fuko la Yosefe analigawa pawiri, Manase ndi Efereimu. Mose sanawagawire malo mabanja a fuko la Levi, koma iwo anangolandira mizinda imene ankakhalamo pamodzi ndi malo amene ankawetako nkhosa ndi ngʼombe zawo. Choncho Aisraeli anagawana dzikolo, monga momwe Yehova analamulira Mose. Apereka Hebroni kwa Kalebe Tsono anthu a fuko la Yuda anabwera kwa Yoswa ku Giligala, ndipo Kalebe mwana wa Yefune Mkeni anati kwa iye, “Inu mukudziwa zimene Yehova ananena kwa Mose munthu wa Mulungu za inu ndi ine ku Kadesi Barinea. Nthawi imene Mose mtumiki wa Yehova anandituma kuchokera ku Kadesi Barinea kudzayendera dzikoli ndinali ndi zaka makumi anayi. Ndipo nditabwerako ndinamuwuza zoona zokhazokha monga momwe ndinaonera. Koma abale anga amene ndinapita nawo anachititsa anthu mantha. Komabe ine ndinamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wonse. Kotero tsiku limenelo Mose anandilonjeza kuti, ‘Dziko limene unayendamo lidzakhala lako ndiponso la ana ako kwamuyaya chifukwa unamvera Yehova Mulungu wanga ndi mtima wako wonse.’ “Tsono papita zaka 45 chiyankhulire Yehova zimenezi kwa Mose. Nthawi imeneyo nʼkuti Aisraeli akuyendayenda mʼchipululu. Yehova wandisunga ndipo tsopano ndili ndi zaka 85. Komabe ndikanali ndi mphamvu lero, monga ndinalili tsiku lija Mose anandituma. Ndili ndi mphamvu moti ndikhoza kupita ku nkhondo kapena kuchita kanthu kena kalikonse. Tsopano ndipatseni dziko la ku mapiri limene Yehova anandilonjeza tsiku lija. Inu munamva nthawi ija kuti Aanaki anali kumeneko ndipo kuti mizinda yawo inali ikuluikulu ndi yotetezedwa. Komabe Yehova atakhala nane ndidzawathamangitsa monga Iye ananenera.” Ndipo Yoswa anadalitsa Kalebe mwana wa Yefune ndi kumupatsa Hebroni kukhala dziko lake. Choncho dera la Hebroni lakhala lili la Kalebe mwana wa Yefune Mkeni mpaka lero chifukwa anamvera Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wonse. (Hebroni ankatchedwa Kiriati Ariba chifukwa cha Ariba amene anali munthu wamphamvu kwambiri pakati pa Aanaki). Ndipo kenaka mʼdziko monse munakhala mtendere. Dziko Limene Yuda Analandira Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni. Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere, kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika. Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera. Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere. Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo, napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani. Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli. Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu. Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu). Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna. Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja. Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu. Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda. Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki). Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake. Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.” Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi. Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili: Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali: Kabizeeli, Ederi, Yaguri Kina, Dimona, Adada Kedesi, Hazori, Itinani Zifi, Telemu, Bealoti, Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori) Amamu, Sema, Molada Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya, Baalahi, Iyimu, Ezemu Elitoladi, Kesili, Horima Zikilagi, Madimena, Sanisana, Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi: Esitaoli, Zora, Asina Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu, Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka, Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi, Dileani, Mizipa, Yokiteeli, Lakisi, Bozikati, Egiloni, Kaboni, Lahimasi, Kitilisi, Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani, Ifita, Asina, Nezibu, Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake. Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake; komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu. Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Mizinda ya kumapiri inali: Samiri, Yatiri, Soko, Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri) Anabu, Esitemo, Animu, Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake. Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani, Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake. Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta Yezireeli, Yokideamu, Zanowa, Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake. Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori, Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake. Mizinda ya ku chipululu inali iyi: Beti-Araba, Midini, Sekaka, Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake. Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo. Madera amene Efereimu ndi Manase Analandira Dziko limene linapatsidwa kwa fuko la Yosefe linayambira ku mtsinje wa Yorodani ku Yeriko, kummawa kwa akasupe a Yeriko, ndiponso kuyambira mtsinje wa Yorodaniwo nʼkumakwera, kudutsa mʼchipululu mpaka ku mapiri a ku Beteli. Kuchokera ku Beteli malire ake anakafika ku Luzi, kudutsa dziko la Ataroti kumene kumakhala Aariki. Malirewo anatsikira cha kumadzulo kwa dziko la Yafuleti mpaka ku chigawo cha kumunsi kwa Beti-Horoni. Kuchokera kumeneko anapitirira mpaka ku Gezeri nʼkuthera ku Nyanja. Choncho Manase ndi Efereimu, ana a Yosefe analandira cholowa chawo. Dziko la mabanja a fuko la Efereimu ndi ili: Malire a dzikolo anachokera kummawa kwa Ataroti Adari mpaka ku mtunda kwa Beti-Horoni. Malirewo anapitirira mpaka ku nyanja. Mikimetati anali kumpoto kwake. Kuchokera kumeneko anakhotera cha kummawa kuloza ku Taanati Silo ndi kudutsa kumeneko cha kummawa mpaka ku Yanowa. Ndipo kuchokera ku Yanowa anatsikira ku Ataroti ndi Naara, nakafika ku Yeriko ndi kukathera ku mtsinje wa Yorodani. Kuchokera ku Tapuwa anapita kumadzulo mpaka ku mtsinje wa Kana ndi kukathera ku nyanja. Dziko ili linali cholowa cha mabanja afuko la Efereimu, kuphatikizapo mizinda yonse ndi midzi yake yopatsidwa kwa Efereimu, koma yokhala mʼkati mwa dziko la Manase. Iwo sanapirikitse Akanaani amene amakhala ku Gezeri ndipo mpaka lero Akanaani akukhala pakati pa Aefereimu koma amagwira ntchito ngati akapolo. Gawo lina la dzikolo linapatsidwa kwa mabanja ena a fuko la Manase, mwana woyamba kubadwa wa Yosefe. Makiri anali mwana woyamba kubadwa wa Manase ndiponso kholo la anthu okhala ku Giliyadi. Popeza kuti iye anali munthu wankhondo, analandira Giliyadi ndi Basani. Mabanja ena otsala a fuko la Manase amene analandira dziko ndi awa: Abiezeri, Heleki, Asirieli, Sekemu, Heferi ndi Semida. Izi ndi zidzukulu zina zazimuna za Manase mwana wa Yosefe ndiponso eni mbumba. Panali Zelofehadi mwana wa Heferi, mwana wa Giliyadi, mwana wa Makiri mwana wa Manase. Iyeyu analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha ndipo mayina awo ndi awa: Mahila, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. Iwo anapita kwa Eliezara wansembe, Yoswa mwana wa Nuni, ndi atsogoleri ndipo anati: “Yehova analamula Mose kuti ife ndi alongo athu atipatse cholowa chathu.” Choncho iwowo pamodzi ndi abale a abambo awo anawapatsa dera lina la dzikolo kuti likhale monga mwa lamulo la Yehova. Choncho kuwonjezera pa mayiko a Giliyadi ndi Basani kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Manase analandiranso magawo khumi chifukwa ana aakazi a fuko la Manase analandira cholowa chawo pakati pa ana aamuna. Dziko la Giliyadi linali dziko la zidzukulu zonse za Manase. Malire a dziko la Manase anayambira ku Aseri, ndipo anakafika ku Mikimetati kummawa kwa Sekemu. Tsono malire anapita kummwera kuloza kwa anthu a ku Eni-Tapuwa. (Manase anatenga dziko la Tapuwa, koma mzinda wa Tapuwawo, umene unali mʼmalire mwa Manase unali wa fuko la Efereimu). Ndipo malire ake anapitirira kummwera mpaka ku mtsinje wa ku Kana. Mizinda ya kummwera kwa mtsinjewo inali ya fuko la Efereimu ngakhale kuti inali mʼdziko la Manase. Malire a fuko la Manase anapita kumpoto kwa mtsinje wa Kana ndi kukathera ku Nyanja. Dziko la kummwera linali la Efereimu ndipo la kumpoto linali la Manase. Dziko la Manase linafika ku nyanja ndipo linachita malire ndi Aseri, kumpoto ndiponso Isakara, kummawa. Mʼdziko la Isakara ndi Aseri, Manase analinso ndi mizinda ya Beti-Seani ndi Ibuleamu pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. Panalinso Akanaani amene ankakhala ku Dori, Endori, Taanaki ndi Megido pamodzi ndi mizinda yozungulira (wachitatu pa mʼndandandawu ndi Nafati Dori). Komabe anthu a fuko la Manase sanathe kuwapirikitsa anthu okhala mʼmizinda imeneyi. Choncho Akanaani anakhalabe mʼmizindayi. Ngakhale Aisraeli anali a mphamvu mʼdzikomo, sanapirikitse Akanaani onse koma anangowasandutsa kukhala akapolo. Anthu a fuko la Yosefe anati kwa Yoswa, “Chifukwa chiyani mwatipatsa gawo limodzi lokha la dziko kuti likhale cholowa chathu? Ife tilipo anthu ambiri popeza Yehova watidalitsa kwambiri.” Yoswa anayankha kuti, “Ngati muli ambiri ndipo dziko la ku mapiri la Efereimu lakucheperani kwambiri, lowani ku nkhalango mudule mitengo, mudzikonzere malo akuti mukhalemo, mʼdziko la Aperezi ndi Arefai.” Tsono zidzukulu za Yosefe zinati, “Dziko la ku mapiri ndi losatikwaniradi, komanso Akanaani onse amene akukhala ku chigwa pamodzi ndi amene akukhala ku Beti-Seani ndi madera awo ndiponso amene ali ku chigwa cha Yezireeli ali ndi magaleta azitsulo.” Koma Yoswa anawuza zidzukulu za Yosefe, za fuko la Efereimu ndi za fuko la Manase kuti, “Inu mulipodi ambiri ndiponso amphamvu. Simulandira gawo limodzi lokha, dziko la ku mapiri lidzakhalanso lanu. Ngakhale kuti ndi nkhalango yokhayokha koma inu mudzadula mitengo yake ndipo lidzakhala lanu mpaka kumapeto. Ngakhale kuti Akanaani ali ndi magaleta azitsulo ndiponso kuti iwo ndi amphamvu, koma inu mudzawapirikitsa.” Kugawa kwa Madera Otsala a Dziko Atagonjetsa dziko lonse Aisraeli anasonkhana ku Silo ndipo anayimikako tenti ya msonkhano. Koma pa nthawiyo nʼkuti mafuko asanu ndi awiri a Aisraeli asanalandire cholowa chawo. Ndipo Yoswa anati kwa Aisraeli, “Kodi mudikira mpaka liti kuti mulowe ndi kulanda dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu wakupatsani? Sankhani amuna atatu kuchokera ku fuko lililonse ndipo ine ndidzawatuma kuti akayendere dzikolo ndi kukalilembera bwino kuti ndiligawe kukhala lawo. Akatero, abwererenso kwa ine. Aligawe dzikolo mʼzigawo zisanu ndi ziwiri; fuko la Yuda lidzakhale ndi dziko lake la kummwera ndi nyumba ya Yosefe ikhalebe mʼdziko lawo la kumpoto. Mudzalembe mawu ofotokoza za zigawo zisanu ndi ziwiri za dzikolo, ndi kubwera nawo kwa ine. Tsono ineyo ndidzakuchitirani maere pamaso pa Yehova Mulungu wanu. Alevi asakhale ndi dziko pakati panu, chifukwa gawo lawo ndi kutumikira Yehova pa ntchito ya unsembe. Ndipo Gadi, Rubeni ndi theka la fuko la Manase analandira kale cholowa chawo kummawa kwa Yorodani. Mose mtumiki wa Yehova ndiye anawapatsa.” Anthuwo akupita kukalembera dzikolo, Yoswa anawalangiza kuti, “Pitani mukayendere ndi kulembera dzikolo. Kenaka mukabwere kwa ine, ndidzakuchitirani maere kuno ku Silo pamaso pa Yehova.” Ndipo anthu anachoka ndi kukayendera dziko lonse. Iwo analemba bwinobwino mʼbuku za dzikolo, mzinda ndi mzinda. Analigawa magawo asanu ndi awiri, ndipo anabwerera kwa Yoswa ku misasa ya ku Silo. Pambuyo pake Yoswa anawachitira maere ku Silo pamaso pa Yehova, ndipo fuko lililonse la Israeli analigawira dziko lake. Dziko la Benjamini Maere anagwera mabanja a fuko la Benjamini. Dziko limene anapatsidwa linali pakati pa fuko la Yuda ndi fuko la Yosefe: Mbali ya kumpoto malire awo anayambira ku Yorodani nalowera chakumpoto kwa matsitso a ku Yeriko kulowera cha kumadzulo kwa dziko la ku mapiri ndi kukafika ku chipululu cha Beti-Aveni. Kuchokera kumeneko malirewo analoza ku Luzi nadutsa mʼmbali mwa mapiri kummwera kwa Luzi (ndiye Beteli) ndipo anatsika mpaka ku Ataroti Adari, ku mapiri a kummwera kwa Beti-Horoni wa Kumunsi. Ndipo malirewo analowanso kwina, analunjika kummwera kuchokera kumadzulo kwake kwa phiri loyangʼanana ndi Beti-Horoni, mpaka ku mzinda wa Kiriyati Baala (ndiye Kiriati Yearimu), mzinda wa anthu a fuko la Yuda. Amenewa ndiye anali malire a mbali ya kumadzulo. Malire a kummwera anayambira mʼmphepete mwenimweni mwa Kiriati Yearimu napita kumadzulo mpaka kukafika ku akasupe a Nefitowa. Malire anatsikira mʼmphepete mwa phiri loyangʼanana ndi chigwa cha Beni Hinomu, kumpoto kwa chigwa cha Refaimu. Anapitirira kutsikira ku chigwa cha Hinomu kummwera kwa chitunda cha Ayebusi mpaka ku Eni Rogeli. Kenaka anakhotera kumpoto kupita ku Eni-Semesi, kupitirira mpaka ku Geliloti amene amayangʼanana ndi pokwera pa Adumimu. Kenaka malire anatsikira ku Mwala wa Bohani, mwana wa Rubeni. Anabzola cha kumpoto kwa chitunda cha Beti Araba ndi kutsikabe mpaka ku chigwa cha Yorodani. Anabzolanso cha kumpoto kwa chitunda cha Beti-Hogila kukafika cha kumpoto ku gombe la Nyanja ya Mchere kumene mtsinje wa Yorodani umathirirako, cha kummwera kwenikweni. Awa anali malire a kummwera. Yorodani ndiye anali malire a mbali ya kummawa. Awa anali malire a dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira. Mabanja a fuko la Benjamini anali ndi mizinda iyi; Yeriko, Beti-Hogila, Emeki Kezizi, Beti-Araba, Zemaraimu, Beteli Avimu, Para, Ofiri, Kefari-Amoni, Ofini ndi Geba, mizinda khumi ndi awiri ndi midzi yake Panalinso Gibiyoni, Rama, Beeroti, Mizipa, Kefira, Moza Rekemu, Iripeeli, Tarala, Zera Haelefu, mzinda wa Ayebusi (ndiye kuti Yerusalemu) Gibeya ndi Kiriati, mizinda 14 ndi midzi yake. Limeneli ndilo dziko limene mabanja a fuko la Benjamini analandira kuti likhale lawo. Dziko la Simeoni Maere achiwiri anagwera mabanja a fuko la Simeoni. Dziko lawo linali mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda. Dzikolo linaphatikiza zigawo izi: Beeriseba (ndi Seba), Molada, Hazari-Suwali, Bala, Ezemu, Elitoladi, Betuli, Horima, Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susa, Beti-Lebaoti ndi Saruheni. Yonse pamodzi inali mizinda 13 ndi midzi yawo. Panalinso mizinda inayi iyi: Aini, Rimoni, Eteri ndi Asani pamodzi ndi midzi yawo. Dzikolo linaphatikizanso midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baalati-Beeri, ndiye kuti Rama wa kummwera. Ili ndi dziko limene mabanja a fuko la Simeoni analandira kukhala lawo. Cholowa cha fuko la Simeoni chinatengedwa kuchokera ku gawo la Yuda chifukwa fuko la Yuda linali lalikulu kwambiri. Izi zinachititsa fuko la Simeoni kukhala mʼkati mwenimweni mwa dziko la Yuda. Dziko la Zebuloni Maere achitatu anagwera mabanja a fuko la Zebuloni: Malire a dziko lawo anafika mpaka ku Saridi. Malirewo anakwera kupita cha kumadzulo ku Marala nakafika ku Dabeseti ndi ku mtsinje wa kummawa kwa Yokineamu. Kuchokera ku mbali ina ya Saridi malire anakhota kupita kummawa ku malire a Kisiloti-Tabori mpaka ku Daberati nakwera mpaka ku Yafiya. Kuchokera kumeneko anabzola kulowa cha kummawa mpaka ku Gati-Heferi ndi ku Eti Kazini ndi kumaloza ku Neya njira ya ku Rimoni. Mbali ya kumpoto malirewo analoza ku Hanatoni ndipo anakathera ku chigwa cha Ifita Eli. Anaphatikizapo Katati, Nahalala, Simironi, Idala ndi Betelehemu. Mizinda yonse inakwana khumi ndi iwiri pamodzi ndi midzi yake. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndi imene mabanja a fuko la Zebuloni analandira. Dziko la Isakara Maere achinayi anagwera mabanja a fuko la Isakara. Dziko lawo linaphatikiza zigawo izi: Yezireeli, Kesuloti, Sunemu, Hafaraimu, Sioni, Anaharati, Rabiti, Kisoni, Ebezi, Remeti, Eni Ganimu, Eni Hada ndi Beti-Pazezi. Malirewa anakafikanso ku Tabori, Sahazuma ndi Beti-Semesi ndipo anakathera ku Yorodani. Mizinda yonse inalipo 16 ndi midzi yake. Mizinda imeneyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Isakara. Dziko la Aseri Maere achisanu anagwera mabanja a fuko la Aseri. Gawo lawo linaphatikiza Helikati, Hali, Beteni, Akisafu, Alameleki, Amadi ndi Misali. Kumadzulo malire anafika ku Karimeli ndi Sihori Libinati. Kenaka anakhotera kummawa kulowera ku Beti-Dagoni nafika ku dziko la Zebuloni ndi ku chigwa cha Ifita Eli, ndipo anapita kumpoto ku Beti-Emeki ndi Neieli. Anapitirirabe kumpoto mpaka kukafika ku Kabuli, Ebroni, Rehobu, Hamoni, ndi Kana, mpaka ku Sidoni Wamkulu. Kenaka malirewo anakhotera ku Rama ndi kupita ku mzinda wotetezedwa wa ku Turo. Kuchokera pamenepo malirewo anakhota kupita ku Hosa nakatulukira ku Nyanja, mʼchigawo cha Akizibu, Uma, Afeki ndi Rehobu. Mizinda yonse inalipo 22 pamodzi ndi midzi yake. Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Aseri. Dziko la Nafutali Maere achisanu ndi chimodzi anagwera mabanja a fuko la Nafutali. Malire awo anayambira ku Helefu mpaka ku mtengo wa thundu wa ku Zaananimu, ndipo anapitirira nʼkukafika ku Adami Nekebu, Yabineeli mpaka ku Lakumi ndi kukathera ku Yorodani. Tsono malirewo anakhotera kumadzulo kupita ku Azinoti-Tabori. Kuchoka kumeneko anapita ku Hukoki, modutsa Zebuloni cha kummwera, Aseri cha kumadzulo ndi mtsinje wa Yorodani cha kummawa. Mizinda yotetezedwa inali Zidimi, Zeri, Hamati, Rakati, Kinereti, Adama, Rama, Hazori, Kedesi, Ederi, Eni Hazori, Yironi, Migidali Eli, Horemu, Beti-Anati ndi Beti-Semesi. Yonse pamodzi inalipo mizinda 19 ndi midzi yake. Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yawo ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Nafutali. Dziko la Dani Maere achisanu ndi chiwiri anagwera mabanja a fuko la Dani. Gawo lawo linaphatikiza mizinda iyi: Zora, Esitaoli, Iri Semesi, Saalabini, Ayaloni, Itira, Eloni, Timna, Ekroni, Eliteke, Gibetoni, Baalati, Yehudi, Beni Beraki, Gati-Rimoni, Me-Yarikoni ndi Rakoni, pamodzi ndi dera loyangʼanana ndi Yopa. Anthu a fuko la Dani atalandidwa dziko lawo, anapita kukathira nkhondo Lesemu. Iwo anapha anthu ake onse, nawulandiratu mzindawo, kuwusandutsa wawo ndi kumakhalamo. Tsono anatcha mzindawo dzina loti Dani popeza ndilo linali dzina la kholo lawo. Mizinda yonseyi pamodzi ndi midzi yake ndiyo inali cholowa cha mabanja a fuko la Dani. Dziko la Yoswa Atatha kugawana zigawo zosiyanasiyana za dzikolo, Aisraeli anamupatsa Yoswa mwana wa Nuni chigawo chake. Potsata zimene Yehova anawalamula, anamupatsa mzinda wa Timnati-Sera umene anawupempha. Mzindawu unali mʼdziko lamapiri la Efereimu. Iye anawumanga mzindawu ndi kukhazikikako. Wansembe Eliezara, Yoswa ndi atsogoleri a mabanja onse a Israeli anagawa dziko lija zigawozigawo pogwiritsa ntchito maere pamaso pa Yehova. Izi zinachitika ku Silo pa khomo la tenti ya msonkhano. Choncho anamaliza kugawa dzikolo. Mizinda Yopulumukiramo Pambuyo pake Yehova anati kwa Yoswa: “Uza Aisraeli kuti apatule mizinda yopulumukiramo, monga ine ndinakulangizira kudzera mwa Mose, kuti aliyense amene wapha munthu mosazindikira osati mwadala azithawirako. Motero adzatetezedwa kwa wolipsira. Ngati munthu wathawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, akafike pa malo oweruzira milandu amene ali pa chipata cha mzindawo ndipo akafotokoze mlandu wake pamaso pa akuluakulu a mzindawo. Kenaka iwo adzamulola kulowa mu mzinda wawo ndi kumupatsa malo woti akhale nawo. Ngati munthu wolipsirayo amutsatira komweko atsogoleriwo asapereke munthu wakuphayo chifukwa anapha Mwisraeli mnzakeyo mosazindikira, osati mwachiwembu. Munthu wakuphayo adzakhalabe mu mzindawo mpaka atayimbidwa mlandu pamaso pa gulu lonse, ndiponso mpaka atamwalira mkulu wa ansembe amene akutumikira pa nthawiyo. Pamenepo munthuyo atha kubwereranso ku mudzi kwawo kumene anachoka mothawa kuja.” Choncho iwo anapatula Kedesi mʼdera la Galileya ku mapiri a Nafutali, Sekemu ku mapiri a Efereimu, ndi Kiriati Ariba (ndiye Hebroni) ku mapiri a Yuda. Kummawa kwa Yorodani, mʼmapiri a chipululu a kummawa kwa Yeriko, anapatula Bezeri pakati pa dera la fuko la Rubeni. Anapatulanso Ramoti ku Giliyadi mʼdera la fuko la Gadi, ndiponso Golani ku Basani mʼdera la fuko la Manase. Imeneyi ndiyo inali mizinda yopulumukiramo ya Aisraeli onse ngakhalenso mlendo wokhala pakati pawo. Munthu aliyense wopha mnzake mwangozi ankathawira ku mizinda imeneyi. Munthu wolipsira sankaloledwa kuti aphe munthu wothawayo ngati mlandu wake sunazengedwe pamaso pa gulu lonse. Mizinda ya Alevi Tsono atsogoleri a mabanja a fuko la Levi anabwera kwa wansembe Eliezara, Yoswa mwana wa Nuni, ndi kwa atsogoleri a mabanja a mafuko onse a Aisraeli, ku Silo mʼdziko la Kanaani ndipo anati, “Yehova analamula kudzera mwa Mose kuti atipatse mizinda kuti tikhalemo, pamodzi ndi malo odyetseramo ziweto zathu.” Choncho, Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizinda iyi pamodzi ndi malo owetera ziweto zawo kuchokera ku madera awo, monga Yehova analamulira: Maere oyamba anagwera mabanja a Kohati, Alevi amene anali zidzukulu za wansembe Aaroni anapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini. Ndipo mabanja otsala a Kohati anapatsidwa mizinda khumi kuchokera ku mafuko a Efereimu, Dani ndi theka la fuko la Manase. Zidzukulu za Geresoni zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mabanja a mafuko a Isakara, Aseri, Nafutali ndi theka la fuko la Manase ku Basani. Mabanja a Merari anapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni. Choncho Aisraeli anapereka kwa fuko la Levi mizindayi pamodzi ndi malo odyetserako ziweto pogwiritsa ntchito maere, monga Yehova analamula kudzera mwa Mose. Awa ndi mayina a mizinda ya mafuko a Yuda ndi Simeoni imene inaperekedwa kwa zidzukulu za Aaroni, ku banja la Kohati amene anali Alevi. Paja maere oyamba anagwera mabanja a Kohati kuti alandira mizinda. Anapatsidwa mzinda wa Kiriati Ariba. (Paja Ariba ndiye kholo la Anaaki). Dzina lina la mzindawu ndi Hebroni, ndipo unali mʼdziko la mapiri la Yuda. Pamodzi ndi mzindawu anapatsidwanso mabusa ake onse ozungulira. Komabe minda ndi midzi yozungulira mizindayi inali itaperekedwa kale kwa Kalebe, mwana wa Yefune kuti ikhale cholowa chake. Choncho zidzukulu za Aaroni wansembe, zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu), Libina, Yatiri, Esitemowa, Holoni, Debri, Aini, Yuta, ndi Beti-Semesi pamodzi ndi mabusa odyetseramo ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda isanu ndi inayi yochokera ku mafuko awiriwa. Fuko la Benjamini linapereka Gibiyoni, Geba, Anatoti ndi Alimoni, pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Choncho mizinda 13 pamodzi ndi malo odyetsera ziweto anapatsidwa kwa ansembe, zidzukulu za Aaroni. Mabanja ena otsalira a Kohati a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Efereimu: Mizinda ya Sekemu ndi Gezeri ndiye inali mizinda wopulumukirako munthu aliyense wopha mnzake mwangozi. Mizindayi inali ku mapiri a Efereimu. Analandiranso mizinda ya Gezeri, Kibuzaimu, Beti-Horoni pamodzi ndi malo odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Fuko la Dani linapereka mizinda ya Eliteke, Gibetoni, Ayaloni, Gati-Rimoni pamodzi ndi mabusa odyetsera ziweto ozungulira mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Kuchokera ku theka la fuko la Manase analandira Taanaki ndi Gati-Rimoni pamodzi ndi malo awo owetera ziweto, mizinda iwiri. Mizinda khumi yonseyi pamodzi ndi malo odyetsera ziweto, zinapatsidwa ku mabanja ena onse a Akohati. Mabanja a Ageresoni a fuko la Levi anapatsidwa mizinda iwiri kuchokera ku theka la Manase wa kummawa, Golani ku Basani (mzinda wopulumukirako amene wapha munthu mwangozi) ndi Beesitera, pamodzi ndi malo awo odyetserako ziweto. Fuko la Isakara linapereka mizinda ya Kisoni, Daberati, Yarimuti ndi Eni Ganimu, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Fuko la Aseri linapereka mizinda ya Misali, Abidoni, Helikati ndi Rehobu pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Fuko la Nafutali linapereka mizinda ya Kedesi wa ku Galileya, mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. Analandiranso mizinda ya Hamoti-Dori ndi Karitani. Kuphatikizira apa, analandira malo odyetsera ziweto a mizindayi. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Mabanja onse a Ageresoni analandira mizinda 13 pamodzi ndi malo awo odyetsera a ziweto. Mabanja a Merari amene anali otsala a fuko la Levi, anapatsidwa mizinda iyi kuchokera ku fuko la Zebuloni: Yokineamu, Karita, Dimuna ndi Nahalali, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Kuchokera ku fuko la Rubeni analandira Bezeri, Yahaza, Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo awo odyetsera ziweto. Yonse pamodzi inali mizinda inayi. Kuchokera ku fuko la Gadi analandira mzinda wa Ramoti ku Giliyadi. Mzinda umene unali wopulumukiramo munthu wopha mnzake mwangozi. Analandiranso mizinda ya Mahanaimu, Hesiboni, Yazeri pamodzi ndi malo odyetserako ziweto ozungulira mizinda yonseyi. Yonse pamodzi inali mizindayi anayi. Choncho mabanja onse a Merari, amene anali otsala a fuko la Levi analandira mizinda khumi ndi iwiri pogwiritsa ntchito maere. Motero mizinda 48 ya mʼdziko limene Aisraeli analanda inapatsidwa kwa Alevi, kuphatikizapo malo ake odyetsera ziweto. Iliyonse mwa mizindayi inali ndi malo owetera ziweto oyizungulira. Motero Yehova anapereka kwa Israeli dziko limene analumbira kulipereka kwa makolo awo. Atalilandira anadzakhalamo. Yehova anawapatsa mtendere mʼdziko lonse monga momwe analonjezera makolo awo. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa adani awo amene anatha kuwagonjetsa chifukwa Yehova anapereka adani awo onse mʼmanja mwawo. Yehova anakwaniritsa zonse zimene analonjeza kwa Aisraeli. Mafuko a Kummawa Abwerera Kwawo Pambuyo pake Yoswa anayitanitsa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase, ndipo anawawuza kuti, “Inu mwachita zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anakulamulani, ndipo mwamvera mu zonse zimene ndinakulamulirani. Aisraeli anzanu simunawasiye nthawi yayitali yonseyi mpaka lero lino. Inu mwaonetsetsa kuti mwachita zonse zimene Yehova anakulamulani. Tsono pakuti Yehova Mulungu wanu wapereka mpumulo kwa abale anu monga anayankhulira nawo, bwererani ku nyumba zanu ku dziko limene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani, dziko limene lili pa tsidya la Yorodani kummawa. Koma samalitsani kuti mumvere malamulo ndi malangizo amene Mose mtumiki wa Yehova anakupatsani: kukonda Yehova Mulungu wanu, kuchita zimene iye amafuna, kumvera malamulo ake, kukhala okhulupirika kwa Iye ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.” Ndipo Yoswa anawadalitsa ndi kuwalola kuti apite ndipo anapitadi ku nyumba zawo. Apa nʼkuti Mose atapereka dziko la Basani ku theka lina la fuko la Manase. Koma theka lina la fuko la Manase Yoswa analipatsa dziko la kumadzulo kwa Yorodani pamodzi ndi abale awo onse. Pamene Yoswa ankawatumiza kwawo anthu amenewa, anawadalitsa, nawawuza kuti, “Mukubwerera kwanu ndi chuma chambiri. Muli ndi ngʼombe zambiri pamodzi ndi siliva, golide, mkuwa ndi chitsulo, ndiponso zovala zambiri. Izi zimene munafunkha kwa adani anu agawireni abale anu.” Choncho mafuko a Rubeni, Gadi, pamodzi ndi theka la fuko la Manase anabwerera kwawo. Aisraeli ena onse anawasiya ku Silo mʼdziko la Kanaani. Tsono anapita ku dziko la Giliyadi, dziko limene linali lawo popeza analilandira potsata malamulo a Yehova kudzera mwa Mose. Atafika ku Geliloti, malo amene ali mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodani mʼdziko la Kanaani, fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase anamanga guwa lansembe lalikulu pamenepo. Ndipo pamene Aisraeli ena onse anawuzidwa kuti anthu a fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase amanga guwa lansembe mʼmalire a Kanaani ku Geliloti, ku tsidya lathu lino la Yorodani, gulu lonse la Aisraeli linasonkhana ku Silo kuti lipite kukachita nawo nkhondo. Choncho Aisraeli anatumiza Finehasi mwana wa wansembe, Eliezara ku dziko la Giliyadi kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase. Pamodzi ndi Finehasiyo anatumiza akuluakulu khumi ochokera ku fuko lililonse la Aisraeli. Aliyense mwa akuluakulu amenewa anali mtsogoleri wa banja limodzi la mafuko a Aisraeli. Atafika ku Giliyadi anawuza fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lija la fuko la Manase kuti, “Gulu lonse likukufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mwachita chinthu chonyansa chotere potsutsana ndi Mulungu wa Israeli? Nʼchifukwa chiyani mwapatuka ndi kuleka kutsata Yehova podzimangira nokha guwa lansembe? Mwapandukiratu Yehova! Kodi tchimo lija la ku Peori ndi lochepa kwa inu? Paja Yehova analanga gulu lonse ndi mliri chifukwa cha tchimolo, ndipo mpaka lero tchimo limene lija tikanazunzika nalobe. Kodi inu tsono mufuna kupatuka kuleka kumutsata Yehova? “ ‘Ngati lero mumupandukira Yehovayo, ndiye kuti mawamawali Iye adzakwiyira gulu lonse wa Israeli. Ngati dziko limene inu mwatenga ndi loyipitsidwa, bwerani ku dziko la Yehova kumene kuli chihema chake kuja, ndipo mukhale nafe limodzi. Koma inu musawukire Yehova kapena kutisandutsa ife kukhala opanduka podzimangira guwa lansembe, kuwonjezera pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. Kumbukirani pamene Akani mwana wa Zera anakana kumvera lamulo la zinthu zoyenera kuwonongedwa, kodi suja mkwiyo wa Yehova unagwera gulu lonse la Israeli? Akaniyo sanafe yekha chifukwa cha tchimo lakelo.’ ” Tsono mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawayankha atsogoleri a mabanja a Israeli aja kuti, “Wamphamvu uja, Mulungu ndiye Yehova! Wamphamvu uja Mulungu ndiye Yehova. Iyeyu ndiye akudziwa chifukwa chiyani tinachita zimenezi. Tikufunanso kuti inu mudziwe. Ngati tinachita izi mopandukira ndiponso moonetsa kusakhulupirira Yehova, lero lomwe lino musatisiye ndi moyo. Ngati tinapandukira Yehova ndi kuleka kumutsata pamene tinadzimangira guwa loti tizipserezerapo nsembe kapena kupereka nsembe zaufa, kapena nsembe za mtendere, Yehova yekha ndiye atilange. “Ayi! Ife tinachita izi kuopa kuti tsiku lina zidzukulu zanu zingadzanene kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Kodi inu mukufuna chiyani kwa Yehova Mulungu wa Israeli? Yehova anayika mtsinje wa Yorodani kukhala malire pakati pa ife ndi inu, anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi. Inuyo mulibe gawo mwa Yehova.’ Tsono mwina zidzukulu zanuzo nʼkudzaletsa zathu kupembedza Yehova. “Nʼchifukwa chake tinaganiza kuti, ‘Tiyeni timange guwa lansembe, koma osati kuti tiziperekapo nsembe zopsereza kapena zopereka.’ Koma mosiyana ndi zimenezi, guwali likhale umboni pakati pa ife ndi inu ndiponso mibado imene ikubwerayo, kuti ife timapembedzanso Yehova ndi nsembe zathu zopsereza, zopereka, ndiponso nsembe za mtendere. Motero mʼtsogolo muno zidzukulu zanu sizidzatha kunena kwa zidzukulu zathu kuti, ‘Inu mulibe gawo mwa Yehova!’ “Ndipo ife tinati kuti, ‘Ngati iwo adzatiyankhulira kapena kuyankhulira zidzukulu zathu motero mʼtsogolo muno, ife tidzayankha kuti, onani guwa lansembe, lofanana ndi lomwe makolo athu anamanga osati loperekerapo nsembe zopsereza kapena nsembe zina koma ngati umboni pakati pa inu ndi ife.’ “Sizingatheke konse kuti ife lero nʼkupandukira Yehova. Ife sitingapatuke kuleka kumutsata Yehova ndi kumanga guwa lina la nsembe zopsereza, nsembe za zakudya, ndi nsembe zina zopikisana ndi guwa la Yehova, Mulungu wathu limene lili patsogolo pa Hema ya Yehova mʼmene amakhalamo.” Tsono Finehasi wansembe ndi atsogoleri a gululo amene anali naye atamva zimene anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka lakummawa la fuko la Manase ananena, anakondwera kwambiri. Ndipo Finehasi wansembe, mwana wa Eliezara anati kwa mafuko a Rubeni, Gadi ndi Manase, “Lero tadziwa kuti Yehova ali nafe chifukwa zimene mwachitazi simunawukire nazo Yehova. Inu mwapulumutsa Aisraeli onse ku chilango cha Yehova.” Ndipo Finehasi mwana wa wansembe Eliezara, pamodzi ndi atsogoleriwo anachoka ku Giliyadi nasiya anthu a fuko la Rubeni ndi Gadi nabwerera ku Kanaani kwa Aisraeli anzawo, ndipo anakafotokoza zonsezi. Mawu amenewa anakondweretsa Aisraeli onse ndipo anayamika Mulungu. Choncho sanakambenso zopita ku nkhondo kukawononga dziko limene Arubeni ndi Agadi ankakhalamo. Arubeni ndi Agadi anatcha guwalo kuti Mboni: Mboni pakati pathu kuti Yehova ndi Mulungu. Kutsanzika kwa Yoswa Panapita nthawi yayitali kuchokera pamene Yehova anakhazikitsa mtendere pakati pa Aisraeli ndi adani awo owazungulira. Nthawi imeneyi nʼkuti Yoswa atakalamba, ali ndi zaka zambiri. Yoswayo anayitanitsa Aisraeli onse pamodzi ndi akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi oyangʼanira anthu antchito ndipo anawawuza kuti, “Ine ndakalamba ndipo ndili ndi zaka zambiri. Inu mwaona zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachita kwa mitundu yonseyi chifukwa cha inu. Ndi Yehova Mulungu wanu amene anakumenyerani nkhondo. Tsono onani! Mitundu ya anthu otsalawa ndayipereka kwa mafuko anu pamodzi ndi mitundu ya anthu ya pakati pa Yorodani ndi Nyanja Yayikulu ya kumadzulo imene ndinayigonjetsa. Yehova Mulungu wanu ndiye adzawathamangitsa pamaso panu. Mudzatenga dziko lawo monga Yehova anakulonjezerani. “Choncho khalani amphamvu, ndipo samalani kuti mumvere zonse zimene zalembedwa mʼbuku la malamulo a Mose. Musapatuke pa malamulo onse amene alembedwamo. Musagwirizane ndi mitundu ya anthu imene yatsala pakati panu. Musatchule mayina a milungu yawo kapena kuyitchula polumbira. Musayitumikire kapena kuyigwadira. Koma mukuyenera kugwiritsa Yehova Mulungu wanu, monga mwachitira mpaka lero lino. “Yehova wapirikitsa patsogolo panu mitundu ya anthu ikuluikulu ndi yolimba. Mpaka lero palibe amene watha kulimbana nanu. Aliyense wa inu atha kuthamangitsa anthu 1,000 chifukwa Yehova Mulungu wanu ndiye amakumenyerani nkhondo, monga momwe analonjezera. Choncho samalitsani kuti mukonde Yehova Mulungu wanu. “Koma ngati mubwerera mʼmbuyo ndi kuphatikizana ndi mitundu yotsalayi imene ili pakati panu ndi kumakwatirana nayo, pamenepo mudziwe kuti Yehova, Mulungu wanu, sadzapirikitsa mitundu imeneyi pamaso panu, koma idzakhala ngati msampha kwa inu kapenanso khwekhwe lokukolani. Idzakhala ngati zikwapu pa msana panu kapenanso ngati minga mʼmaso mwanu mpaka mutatha psiti mʼdziko labwinoli limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani. “Aliyense wa inu akudziwa mu mtima mwake komanso mʼmoyo mwake kuti zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu anakulonjezani zachitika. Palibe lonjezo ndi limodzi lomwe limene silinakwaniritsidwe. Monga momwe Yehova Mulungu wanu wakuchitirani zabwino zonse zimene ananena kuti adzachita, Yehovayo angathenso kukuchitirani zoyipa zonse zimene waopseza, mpaka kukuchotsani mʼdziko lokoma limene anakupatsani. Ngati muphwanya pangano la Yehova Mulungu wanu, limene anakulamulirani nʼkumapita kukatumikira milungu ina ndi kuyigwadira, Yehova adzakukwiyirani, ndiye mudzachotsedwa mʼdziko labwinoli limene Yehova wakupatsani.” Kukonzanso Pangano ku Sekemu Tsono Yoswa anasonkhanitsa mafuko onse a Israeli ku Sekemu. Iye anayitanitsa akuluakulu, atsogoleri, oweruza, ndi akuluakulu a boma la Israeli, ndipo iwo anafika pamaso pa Mulungu. Yoswa anati kwa anthu onse, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Kalekale makolo anu, kuphatikiza Tera, abambo a Abrahamu ndi Nahori ankakhala kutsidya kwa Mtsinje ndipo ankapembedza milungu ina. Koma ine ndinatenga kholo lanu Abrahamu kumuchotsa ku dziko la kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate ndipo ndinamutsogolera kupita ku dziko la Kanaani. Ndinamupatsa zidzukulu zambiri. Ndinamupatsa Isake, ndipo Isake ndinamupatsa Yakobo ndi Esau. Ndinapereka dziko la mapiri la Seiri kwa Esau, koma Yakobo ndi ana ake anapita ku Igupto. “ ‘Kenaka ndinatuma Mose ndi Aaroni, ndipo ine ndinazunza Aigupto. Pambuyo pake ndinakutulutsani. Nditatulutsa makolo anu ku Igupto ndinafika nawo ku Nyanja Yofiira. Aigupto anawathamangira ndi magaleta ndi okwera pa akavalo mpaka ku Nyanja Yofiira. Tsono makolo anuwo anapemphera kwa Ine kuti ndiwathandize, ndipo ndinayika mtambo wakuda pakati pawo ndi Aiguptowo, ndipo Nyanja inamiza Aigupto aja. Inu munaona ndi maso anu zimene ndinachita kwa Aiguptowo ndipo inu munakhala mʼchipululu nthawi yayitali. “ ‘Pambuyo pake Ine ndinabwera nanu ku dziko la Aamori amene amakhala kummawa kwa Yorodani. Iwo anamenyana nanu koma ndinawapereka mʼdzanja lanu. Ndinawawononga pamaso panu, ndipo inu munalanda dziko lawo. Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu, analimbana ndi Israeli. Iye anayitanitsa Balaamu mwana wa Beori kuti akutemberereni. Koma ine sindinamvere Balaamu, kotero iye anakudalitsani mowirikiza ndipo ndinakulanditsani mʼdzanja lake. “ ‘Ndipo inu munawoloka Yorodani ndi kufika ku Yeriko. Anthu a ku Yeriko analimbana nanu pamodzi ndi Aamori, Aperezi, Akanaani, Ahiti, Agirigasi, Ahivi ndi Ayebusi. Koma Ine ndinawapereka mʼdzanja lanu. Ine ndinatumiza mavu amene anapirikitsa mafumu awiri Aamori aja pamaso panu. Inu simunachite izi ndi lupanga ndi uta wanu. Motero ndinakupatsani dziko limene simunalivutikire ndiponso mizinda imene simunamange. Inu mukukhala mʼmenemo ndi kumadya zipatso za mʼmunda wamphesa ndi kuthyola zipatso mʼmitengo ya olivi zimene simunadzale.’ “Ndipo tsopano wopani Yehova ndi kumutumikira Iye mokhulupirika ndi moona. Chotsani milungu imene makolo anu ankapembedza kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate ndi ku Igupto ndipo tumikirani Yehova. Koma ngati kutumikira Yehova kukuyipirani, sankhani lero amene mudzamutumikire, kapena milungu imene makolo anu ankayitumikira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, kapena milungu ya Aamori, amene mukukhala mʼdziko lawo. Koma ine ndi banja langa, tidzatumikira Yehova.” Ndipo anthu anayankha, “Sizingatheke kuti timusiye Yehova ndi kutumikira milungu ina! Yehova Mulungu wathu ndiye amene anatitulutsa ife ndi makolo athu mu ukapolo, mʼdziko la Igupto. Tinaona ndi maso athu zizindikiro zozizwitsa zimene anachita. Iye anatiteteza pa ulendo wathu wonse ndi pakati pa mitundu yonse imene tinkakumana nayo. Ife tikufika Iye anapirikitsa anthu onse pamodzi ndi Aamori amene ankakhala mʼdzikoli. Ifenso tidzatumikira Yehova chifukwa Iye ndiye Mulungu.” Koma Yoswa anati kwa anthuwo, “Inutu simungathe kutumikira Yehova. Iye ndi Mulungu woyera, salola kupikisana naye. Sadzakukhululukirani ngati mumuwukira ndi kumuchimwira. Ngati inu musiya Yehova ndi kutumikira milungu yachilendo, adzakufulatirani. Iye adzakulangani ndi kukuwonongani ngakhale kuti poyamba anakuchitirani zabwino.” Koma anthuwo anati kwa Yoswa, “Ayi! Ife tidzatumikira Yehova.” Kenaka Yoswa anati, “Inu mukudzichitira nokha umboni kuti mwasankha kutumikira Yehova.” Iwo anayankha kuti, “Inde ife ndife mboni.” Yoswa anati, “Tsono chotsani milungu yachilendo imene ili pakati panu ndipo perekani mitima yanu kwa Yehova Mulungu wa Israeli.” Ndipo anthuwo anati kwa Yoswa, “Ife tidzatumikira Yehova Mulungu wathu ndi kumvera Iye.” Choncho pa tsiku limenelo Yoswa anachita pangano mʼmalo mwa anthuwo, ndipo pa Sekemu pomwepo iye anapereka malamulo ndi malangizo kwa anthu aja. Ndipo Yoswa analemba zinthu izi mʼbuku la malamulo a Mulungu. Kenaka iye anatenga mwala waukulu nawuyimika pansi pa mtengo wa thundu pa malo wopatulika a Yehova. Yoswa anati kwa anthu onse, “Tamvani! Mwala uwu udzakhala mboni yotitsutsa. Mwalawu wamva mawu onse amene Yehova wayankhula kwa ife. Udzakhala mboni yotitsutsa ngati mukhala osakhulupirika kwa Mulungu wanu.” Kumwalira kwa Yoswa ndi Eliezara Kenaka Yoswa analola anthu kuti apite, aliyense ku dera lake. Zitatha zinthu izi, Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110, ndipo anamuyika mʼmanda mʼdziko lake, ku Timnati-Sera dziko lamapiri la ku Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. Israeli anatumikira Yehova pa nthawi yonse imene Yoswa anali ndi moyo ndiponso pa nthawi ya akuluakulu amene anali moyo Yoswa atamwalira, anthu amene ankadziwa zonse zimene Yehova anachitira Israeli. Ndipo mafupa a Yosefe amene Aisraeli anawatulutsa ku Igupto anawayika mʼmanda a ku Sekemu pa malo amene Yakobo anagula ndi ndalama zasiliva 100 kwa ana a Hamori, abambo a Sekemu. Malo awa anakhala cholowa cha adzukulu a Yosefe. Ndipo Eliezara mwana wa Aaroni anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda ku Gibeya, malo amene anapatsidwa kwa Finehasi mwana wake, mʼdziko lamapiri la Efereimu.