- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 YONA Yona Yona Jnh Yona Yona Athawa Yehova Yehova anayankhula ndi Yona mwana wa Amitai kuti, “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire motsutsana nawo, chifukwa zoyipa zawo zafika pamaso panga.” Koma Yona anathawa Yehova ndi kulowera ku Tarisisi. Anapita ku Yopa, kumene anapeza sitima yapamadzi yopita ku Tarisisi. Atagula chiphaso, anakwera sitimayo kupita ku Tarisisi kuthawa Yehova. Koma Yehova anatumiza chimphepo champhamvu pa nyanja, ndipo panauka namondwe wamphamvu amene anafuna kuphwanya sitimayo. Onse oyendetsa sitimayo anachita mantha ndipo aliyense anayamba kupemphera kwa mulungu wake. Ndipo anaponya katundu mʼnyanja kuti sitimayo ipepuke. Koma Yona pa nthawiyi nʼkuti atatsikira mʼkatikati mwa sitimayo kumene anagona tulo tofa nato. Mkulu wa oyendetsa sitimayo anapita kwa iye ndipo anati, “Kodi iwe, nʼchifukwa chiyani ukugona? Dzuka pemphera kwa mulungu wako! Mwina adzatithandiza, ndipo sitidzawonongeka.” Ndipo oyendetsa sitimayo anayamba kuwuzana kuti, “Bwerani, tichite maere kuti tipeze amene wabweretsa tsoka limeneli.” Iwo anachita maerewo ndipo anagwera Yona. Tsono anamufunsa kuti, “Tatiwuze, tsoka limeneli latigwera chifukwa chiyani? Umagwira ntchito yanji? Ukuchokera kuti? Kwanu nʼkuti? Ndiwe mtundu wanji wa anthu?” Iye anayankha kuti, “Ndine Mhebri, ndipo ndimapembedza Yehova, Mulungu Wakumwamba, amene analenga nyanja ndi mtunda.” Izi zinawachititsa mantha kwambiri ndipo anafunsa kuti, “Kodi wachita chiyani?” (Iwo ankadziwa kuti iyeyo amathawa Yehova, chifukwa nʼkuti atawawuza kale). Namondwe ananka nakulirakulirabe pa nyanjapo. Tsono anamufunsa iye kuti, “Kodi tikuchite chiyani kuti nyanjayi ikhale bata?” Iye anayankha kuti, “Nyamuleni ndi kundiponya mʼnyanjamu ndipo nyanjayi ikhala bata. Ndikudziwa kuti wolakwa ndine nʼchifukwa chake chimphepo champhamvuchi chabwera pa inu.” Komabe oyendetsa sitimayo anayesetsa kupalasa kwambiri kuti abwerere ku mtunda koma analephera ndithu poti nyanja inawinduka kwambiri kuposa poyamba paja Pamenepo iwo anafuwulira kwa Yehova nati, “Inu Yehova, musalole kuti ife tife chifukwa cha moyo wa munthu uyu. Musatizenge mlandu wa kupha munthu wosalakwa, pakuti ife tachita monga mwakufuna kwanu, Inu Yehova.” Ndipo anatenga Yona namuponya mʼnyanja, ndipo nyanja yowindukayo inakhala bata. Anthuwo ataona zimenezi anachita mantha akulu ndi Yehova, ndipo anapereka nsembe kwa Yehova nalumbira kuti adzatumikira Yehovayo. Koma Yehova anatuma nsomba yayikulu kuti imeze Yona. Motero Yona anakhala mʼmimba mwa nsombayo masiku atatu, usana ndi usiku. Pemphero la Yona Yona ali mʼmimba mwa chinsomba chija anapemphera kwa Yehova Mulungu wake. Iye anati: “Pamene ndinali mʼmavuto anga ndinayitana Yehova, ndipo Iye anandiyankha. Ndili ku dziko la anthu akufa ndinapempha thandizo, ndipo Inu munamva kulira kwanga. Munandiponya mʼnyanja yozama, mʼkati mwenimweni mwa nyanja, ndipo madzi oyenda anandizungulira; mafunde anu onse ndi mkokomo wake zinandimiza. Ndinati, ‘Ine ndachotsedwa pamaso panu; komabe ndidzayangʼananso ku Nyumba yanu yopatulika.’ Madzi wondimiza anandichititsa mantha, nyanja yozama inandizungulira; udzu wa mʼmadzi zinakuta mutu wanga. Ndinatsikira kunsi ndithu, mʼtsinde mwa mapiri; mipiringidzo ya dziko inanditsekereza kosatha. Koma Inu munatulutsa moyo wanga mʼmandamo, Inu Yehova Mulungu wanga. “Pamene moyo wanga umachoka mwa ine, ine ndinakumbukira Inu Yehova, ndipo pemphero langa linafika kwa inu, ku Nyumba yanu yopatulika. “Iwo amene amagwiritsitsa mafano achabechabe amataya chisomo chawo. Koma ine ndidzapereka kwa Inu nsembe ndikuyimba nyimbo yamayamiko. Chimene ndinalonjeza ndidzachikwaniritsa. Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.” Ndipo Yehova analamula chinsomba chija, ndipo chinakamusanza Yonayo mʼmbali mwa nyanja. Yona Apita ku Ninive Ndipo Yehova anayankhula ndi Yona kachiwiri kuti, “Nyamuka, pita ku mzinda waukulu wa Ninive ndipo ukalalikire uthenga umene ndikupatsa.” Yona anamvera mawu a Yehova ndipo anapita ku Ninive. Tsono Ninive unali mzinda waukulu kwambiri; wofunika masiku atatu kuwudutsa. Yona analowa mu mzindawo, nayenda ulendo wa tsiku limodzi. Iye ankalalikira kuti, “Atsala masiku makumi anayi kuti Ninive awonongedwe.” Anthu a ku Ninive anakhulupirira Mulungu. Analengeza kuti aliyense, wamkulu ndi wamngʼono yemwe asale zakudya ndipo avale chiguduli. Mfumu ya ku Ninive itamva nkhaniyi, inatsika pa mpando wake waufumu, nivula mkanjo wake waufumu ndipo inavala chiguduli ndi kukhala pansi pa fumbi. Tsono mfumuyo inalengeza mu Ninive kuti, “Mwa lamulo lochokera kwa mfumu ndi akalonga ake: “Munthu aliyense kapenanso nyama, ngʼombe kapena nkhosa, zisadye kanthu kalikonse; musazilole kuti zidye kapena kumwa. Koma anthu avale ziguduli, ndipo nyamanso aziveke ziguduli. Munthu aliyense azifuwula kwa Mulungu ndi mphamvu zake zonse. Anthuwo asiye makhalidwe awo oyipa ndi machitidwe achiwawa. Angadziwe ndani? Mwina Mulungu nʼkutikhululukira ndipo mwa chifundo chake nʼkuleka kutikwiyira, ifeyo osawonongedwa.” Mulungu ataona zimene anthuwo anachita, ndi mmene anasiyira makhalidwe awo oyipa, anawachitira chifundo ndipo sanabweretse chiwonongeko chimene anawaopseza nacho. Mkwiyo wa Yona ndi Chifundo cha Yehova Koma Yona anakhumudwa kwambiri ndipo anakwiya. Iye anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kodi izi si zimene ndinanena ndikanali kwathu? Nʼchifukwa chaketu ine ndinafulumira kuthawa kupita ku Tarisisi. Ine ndinadziwa kuti ndinu Mulungu wokoma mtima ndi wachifundo, wosakwiya msanga ndi wa chikondi chopanda malire, Mulungu amene mumaleka kubweretsa tsoka. Ndipo tsopano, Inu Yehova, ingondiphani basi, pakuti ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.” Koma Yehova anayankha kuti, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye?” Yona anatuluka mu mzindamo nakakhala pansi cha kummawa kwa mzindawo. Kumeneko anadzimangira chithando nakhala mʼmenemo mu mthunzi, kudikira kuti aone zimene zichitikire mzindawo. Tsono Yehova Mulungu anameretsa msatsi ndi kuyikulitsa kuti ipereke mthunzi kwa Yona kuchotsa mavuto ake; ndipo Yona anasangalala kwambiri chifukwa cha msatsiyo. Koma tsiku linalo mmawa, Mulungu anabweretsa mbozi imene inadya msatsiyo ndipo inafota. Dzuwa litatuluka, Yehova anabweretsa mphepo yotentha yochokera kummawa, ndipo dzuwa linatentha pamutu pa Yona kotero analenguka nalo. Iye anangofuna atafa, ndipo anati, “Ndi bwino kuti ndife kupambana nʼkukhala ndi moyo.” Koma Mulungu anati kwa Yona, “Kodi nʼkoyenera kuti iwe ukwiye chifukwa cha msatsi?” Iye anayankha kuti, “Inde nʼkoyenera. Kukwiya kwanga nʼkofuna kufa nako.” Koma Yehova anati, “Iwe ukumvera chisoni msatsiwo, ngakhale kuti sunawugwirire ntchito kapena kuwukulitsa. Inamera pa usiku umodzi ndipo inafanso pa usiku umodzi. Koma mu Ninive muli anthu opitirira 120,000 amene sadziwa kusiyanitsa kuti chabwino nʼchiti ndipo choyipa nʼchiti, mulinso ziweto zochuluka. Kodi sindiyenera kumvera chisoni mzinda waukulu ngati uwu?”