- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 YOBU Yobu Yobu Yobu Yobu Mawu Oyamba Mʼdziko la Uzi munali munthu wina, dzina lake Yobu. Munthu ameneyu anali wosalakwa ndi wolungama mtima, ankaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. Anali ndi ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu, ndipo anali ndi nkhosa 7,000, ngamira 3,000, ngʼombe zantchito 1,000 ndi abulu aakazi 500, ndiponso anali ndi antchito ambiri. Iye anali munthu wotchuka kwambiri pakati pa anthu onse a mʼmayiko a kummawa. Ana ake aamuna ankachita phwando mosinthanasinthana mʼnyumba zawo, ndipo ankayitana alongo awo atatu aja kudzadya ndi kumwa nawo. Masiku aphwandowo atatha, Yobu ankawayitana kuti adzawayeretse. Mmamawa iye ankapereka nsembe yopsereza kuperekera mwana aliyense, poganiza kuti, “Mwina ana anga achimwa ndi kutukwana Mulungu mʼmitima yawo.” Umu ndi mmene Yobu ankachitira nthawi zonse. Yobu Ayesedwa Koyamba Ana a Mulungu atabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anafika nawo limodzi. Yehova anati kwa Satanayo, “Kodi iwe ukuchokera kuti?” Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.” Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa.” Satana anayankha kuti, “Kodi Yobu amaopa Mulungu popanda chifukwa?” “Kodi Inu simumamuteteza iyeyo, nyumba yake ndi zonse zimene ali nazo? Mwadalitsa ntchito ya manja ake, kotero kuti nkhosa ndi ngʼombe zake zili ponseponse mʼdzikomo. Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kukantha zonse ali nazo ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.” Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, tsono zonse zimene ali nazo ndaziyika mʼmanja mwako, koma iye yekhayo usamukhudze.” Pamenepo Satana anachoka pamaso pa Yehova. Tsiku lina pamene ana aamuna ndi ana aakazi a Yobu ankachita phwando ndi kumwa vinyo mʼnyumba mwa mkulu wawo, wamthenga anabwera kwa Yobu ndipo anati, “Ngʼombe zanu zotipula ndipo abulu anu amadya chapafupi pomwepo, tsono panabwera Aseba kudzatithira nkhondo ndi kutenga zonse. Apha antchito ndi lupanga, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!” Iyeyo akuyankhulabe, wamthenga wina anabwera nati, “Kunagwa mphenzi ndipo yapsereza nkhosa ndi antchito anu onse, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!” Iyeyo akuyankhulabe, wamthenga wina anabwera nati, “Akasidi anadzigawa mʼmagulu atatu ankhondo ndipo anafika pa ngamira zanu ndi kuzitenga. Apha antchito anu onse ndi lupanga, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!” Iyeyo akuyankhulabe, panafikanso wamthenga wina nati, “Ana anu aamuna ndi aakazi amachita phwando ndi kumwa vinyo mʼnyumba ya mkulu wawo, mwadzidzidzi chinayamba chimphepo champhamvu chochokera ku chipululu, nʼkudzawomba nyumba mbali zonse zinayi. Nyumbayo yawagwera ndipo afa, ndipo ine ndekha ndiye ndapulumuka kuti ndidzakuwuzeni!” Atamva zimenezi, Yobu anayimirira nangʼamba mkanjo wake, ndi kumeta tsitsi lake. Kenaka anadzigwetsa pansi napembedza Mulungu, nati, “Ndinatuluka maliseche mʼmimba mwa amayi anga, namonso mʼmanda ndidzalowa wamaliseche. Yehova ndiye anapereka ndipo Yehova watenga; litamandike dzina la Yehova.” Mu zonsezi, Yobu sanachimwe kapena kunena kuti, “Mulungu walakwa.” Yobu Ayesedwa Kachiwiri Tsiku linanso pamene ana a Mulungu anabwera kudzadzionetsa pamaso pa Yehova, nayenso Satana anabwera nawo limodzi kudzadzionetsa pamaso pa Yehova. Ndipo Yehova anati kwa Satana, “Kodi iwe ukuchokera kuti?” Satana anayankha Yehova kuti, “Ndakhala ndikungoyendayenda ndi kumangozungulira mʼdzikoli.” Pamenepo Yehova anati kwa Satana, “Kodi unalingalirapo za mtumiki wanga Yobu? Palibe wina pa dziko lapansi wofanana naye; ndi munthu wosalakwa ndi wolungama mtima, munthu amene amaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa. Ndipo iye akanalibe wangwiro, ngakhale iwe unandiwumiriza kuti ndikulole kuti umuvutitse popanda chifukwa.” Satana anayankha kuti, “Iye ayesedwe mʼthupi mwake. Munthu angathe kupereka zonse ali nazo malingana iyeyo ali ndi moyo. Koma tatambasulani dzanja lanu ndi kuwononga thupi lake, ndipo iyeyo adzakutukwanani ndithu pamaso panu.” Yehova anati kwa Satana, “Chabwino, iye ali mʼmanja mwako; koma moyo wake usawuchotse.” Choncho Satana anachoka pamaso pa Yehova napita kukazunza Yobu ndi zilonda zaululu pa thupi lake lonse. Pamenepo Yobu anatenga phale ndi kumadzikanda nalo atakhala pa dzala la phulusa. Mkazi wake anati kwa iye, “Kodi ukuwumirirabe kukhala wangwiro? Tukwana Mulungu kuti ufe!” Yobu anayankha kuti, “Ukuyankhula ngati mkazi wopusa. Kodi tidzalandira zokoma zokhazokha kwa Mulungu, osalandiranso zowawa?” Mu zonsezi, Yobu sanachimwe pa zimene anayankhula. Abwenzi Atatu a Yobu Abwenzi atatu a Yobu, Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama, atamva za tsoka lonse limene linamugwera iye, ananyamuka ku nyumba zawo nakumana malo amodzi mopangana kuti apite ndi kukamupepesa Yobu ndi kumutonthoza. Atamuona Yobuyo, iwo ali chapatalipo, sanathe kumuzindikira. Choncho anayamba kulira mokweza mawu ndipo anangʼamba mikanjo yawo ndi kuwaza fumbi pa mitu yawo. Tsono anakhala naye pamodzi pansi kwa masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku omwe. Palibe ndi mmodzi yemwe anayankhula naye, chifukwa anazindikira kuti Yobu amavutika kwambiri. Mawu a Yobu Pambuyo pake Yobu anatsekula pakamwa pake nayamba kutemberera tsiku limene iyeyo anabadwa. Ndipo Yobu anati: “Tsiku limene ine ndinabadwa litembereredwe ndi usiku umene ananena kuti, ‘Mwana wamwamuna wabadwa!’ Tsiku limenelo lisanduke mdima; Mulungu wa kumwambako asalilabadirenso; kuwala kusaonekenso pa tsikulo. Mdima ndi mthunzi wa imfa zikhale pa tsiku limeneli; mtambo uphimbe tsikuli; mdima wandiweyani udetse kuwala kwake. Usiku umenewo ukutidwe ndi mdima wandiweyani; usawerengedwenso pamodzi ndi masiku a chaka, kapena kukhala pa mwezi wina uliwonse. Usiku umenewo usabweretse chilichonse chabwino; kusamvekenso nthungululu za chikondwerero. Odziwa kutemberera masiku alitemberere tsikulo, iwo amene akonzekera kuwutsa Leviyatani. Nyenyezi zake za mʼbandakucha zikhale mdima; tsikulo liyembekezere kucha pachabe ndipo lisaonenso kuwala koyamba kwa mʼbandakucha. Pakuti tsiku limenelo ndiye ndinatuluka mʼmimba ya amayi anga ndipo ndi limene linandionetsa zovuta. “Bwanji ine sindinawonongeke pamene ndinkabadwa ndi kufa pamene ndimatuluka mʼmimba? Chifukwa chiyani panali mawondo wondilandirirapo ndi mawere woti andiyamwitsepo? Pakuti tsopano bwenzi ndili gone mwamtendere; ndikanakhala nditagona tulo ndili pa mpumulo pamodzi ndi mafumu ndi aphungu a dziko lapansi, amene anadzimangira nyumba zikuluzikulu zimene tsopano ndi mabwinja, pamodzi ndi olamulira amene anali ndi golide, amene anadzaza nyumba zawo ndi siliva. Kapena, bwanji sindinakwiriridwe pansi monga mwana wobadwa wakufa kale, ngati khanda limene silinaone kuwala kwa dzuwa? Ku mandako anthu oyipa sakhalanso pa mavuto, ndipo kumeneko anthu otopa ali pa mpumulo. A mʼndende kumeneko akusangalala ndi mtendere; sakumvanso mawu ofuwula a kapitawo wa akapolo. Anthu wamba ndi anthu apamwamba ali kumeneko, ndipo kapolo ndi womasuka kwa mbuye wake. “Chifukwa chiyani dzuwa limawalira iwo amene ali pa mavuto, ndipo moyo umapatsidwa kwa owawidwa mtima, kwa iwo amene amalakalaka imfa imene sibwera, amene amayifunafuna imfayo kupambana chuma chobisika, amene amakondwa ndi kusangalala akamalowa mʼmanda? Chifuwa chiyani moyo umaperekedwa kwa munthu amene njira yake yabisika, amene Mulungu wamuzinga ponseponse? Mʼmalo moti ndidye, ndimalira, ndi kubuwula kwanga nʼkosalekeza. Chimene ndinkachiopa chandigwera; chimene ndinkachita nacho mantha chandichitikira. Ndilibe mtendere kapena bata, ndilibe mpumulo, koma mavuto okhaokha.” Mawu a Elifazi Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti, “Ngati wina atakuyankha, kodi ungakhumudwe? Koma ndani angakhale chete wosayankhula? Taganiza momwe iwe walangizira anthu ambiri, momwe walimbitsira anthu ofowoka. Mawu ako analimbitsa anthu ofuna kugwa; unachirikiza anthu wotha mphamvu. Koma tsopano mavuto akufikira ndipo wataya mtima, zakukhudza ndipo uli ndi mantha. Kodi kuopa Mulungu kwako sindiko kulimbika mtima kwako? Ndipo moyo wako wosalakwa ndiye chiyembekezo chako? “Ganiza bwino tsopano: Kodi munthu wosalakwa anawonongekapo nʼkale lonse? Nʼkuti kumene munthu wolungama mtima anaphedwa? Monga ndaonera ine, anthu amene amatipula zoyipa, ndi iwo amene amadzala mavuto, amakolola zomwezo. Iwo amaphedwa ndi mpweya wa Mulungu; amawonongeka ndi mpweya waukali wa mkwiyo wake. Mikango imabangula ndi kulira, komabe mano a mikango yamphamvu amathyoledwa. Mkango umafa chifukwa chosowa nyama, ndipo ana amkango amamwazikana. “Mawu anabwera kwa ine mwamseri, makutu anga anamva kunongʼona kwake. Mʼkati mwa maloto ochititsa mantha usiku, nthawi imene anthu amagona tulo tofa nato, ndinagwidwa ndi mantha, ndi kuyamba kunjenjemera ndipo mafupa anga onse anaweyeseka. Pamenepo mzimu unadutsa pamaso panga, ndipo ubweya wa pa thupi langa unayima kuti njoo. Chinthucho chinayimirira koma sindinathe kuzindikira kuti chinali chiyani. Chinthu chinayima patsogolo panga, kunali zii ndipo ndinamva mawu akuti, ‘Kodi munthu angathe kukhala wolungama kupambana Mulungu? Kodi munthu angathe kukhala wangwiro kupambana Mlengi wake? Ngati Mulungu sakhulupirira atumiki ake omwe, ngati Iye amawapeza angelo ake ndi cholakwa, nanga kuli bwanji ndi iwo amene amakhala mʼnyumba zadothi, amene maziko awo ndi fumbi, amene amathudzuka mosavuta ngati kadziwotche! Mmawa ali moyo, pofika madzulo afa; mwakachetechete, amawonongeka kwamuyaya. Kodi zonse zimene ali nazo sizimatheratu, kotero kuti amafa osadziwa nʼkanthu komwe?’ “Itana ngati ungathe, koma ndani adzakuyankhe? Kodi ndi kwa mngelo uti ungapezeko thandizo? Mkwiyo umapha chitsiru, ndipo njiru imawononga wopusa. Ine ndinaona chitsiru chitamera mizu, koma mwadzidzidzi nyumba yake inatembereredwa. Ana ake alibe ndi chitetezo chomwe; amaponderezedwa mʼbwalo la milandu popanda owateteza. Anthu anjala amamudyera zokolola zake, amamutengera ndi za pa minga pomwe, ndipo anthu akhwinthi amafunkha chuma chake. Pakuti masautso satuluka mʼfumbi, ndipo kuwukira sikuchokera mʼdothi. Komatu munthu amabadwira kuti azunzike monga momwe mbaliwali zimathethekera mlengalenga. “Koma ndikanakhala ine, ndikanamudandawulira Mulungu; ndikanapereka mlandu wanga kwa Iye. Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingatheke kuwerengedwa. Iye amagwetsa mvula pa dziko lapansi, ndipo amathirira minda ya anthu. Iye amakweza anthu wamba, ndipo iwo amene akulira amawayika pa malo otetezedwa. Iyeyo amalepheretsa chiwembu cha anthu ochenjera, kotero kuti cholinga chawo sichipindula kanthu. Iye amakola anthu ochenjera mu msampha wa kuchenjera kwawo, ndipo zolinga za atambwali amazithetsa msangamsanga. Mdima umawagwera nthawi yamasana; nthawi yamasana amayenda moyambasayambasa monga nthawi ya usiku. Mulungu amapulumutsa amphawi ku lupanga la mʼkamwa mwawo; amawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amphamvu. Choncho osauka ali ndi chiyembekezo, ndipo anthu opanda chilungamo amawatseka pakamwa. “Wodala munthu amene Mulungu amamudzudzula; nʼchifukwa chake usanyoze chilango cha Wamphamvuzonse. Pakuti Iye amavulaza koma amamanganso mabalawo; Iye amakantha munthu, komanso manja ake amachiritsa. Pakuti adzakupulumutsa ku masautso nthawi ndi nthawi, mavuto angachuluke bwanji, sadzakukhudza ndi pangʼono pomwe. Pa nthawi ya njala adzakulanditsa ku imfa, ndipo nthawi ya nkhondo adzakupulumutsa ku lupanga. Adzakuteteza kwa anthu osinjirira, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha pamene chiwonongeko chafika. Uzidzaseka pa nthawi ya chiwonongeko ndi ya njala, ndipo palibe chifukwa chochitira mantha ndi zirombo za mʼdziko lapansi. Pakuti udzachita pangano ndi miyala ya mʼmunda mwako, ndipo nyama zakuthengo zidzakhala nawe mwamtendere. Udzadziwa kuti nyumba yako ndi malo otetezedwa; udzawerengera katundu wako ndipo sudzapeza kanthu kamene kasowapo. Udzadziwa kuti ana ako adzakhala ambiri, ndipo zidzukulu zako zidzakhala ngati udzu wa mʼdziko lapansi. Udzafika ku manda utakalamba, monga mitolo ya zokolola pa nyengo yake. “Ife tafufuza zimenezi ndipo ndi zoona, choncho uzimvere ndi kuzitsata.” Mawu a Yobu Tsono Yobu anayankha kuti, “Achikhala mavuto anga anayezedwa, ndipo zipsinjo zanga zonse zikanayikidwa pa sikelo! Ndithu, zikanalemera kupambana mchenga wa ku nyanja; nʼchifukwa chake mawu anga akhala okhadzula. Mivi ya Wamphamvuzonse yandibaya, thupi langa likumva ululu wa miviyo; zoopsa za Mulungu zandizinga. Kodi bulu wakuthengo amalira akakhala ndi msipu, nanga ngʼombe imalira ikakhala ndi chakudya? Kodi chakudya chosakoma nʼkuchidya chopanda mchere, nanga choyera cha dzira chimakoma? Zakudya zimenezi sindifuna nʼkuzilawa komwe; zakudya zimenezi zimabwerera kukhosi. “Aa, ndikanalandira chimene ndikuchipempha, chikhala Mulungu anandipatsa chimene ndikuchiyembekezera, achikhala chinamukomera Mulungu kuti anditswanye, kulola dzanja lake kuti lindimenye ndi kundiwonongeratu! Pamenepo ine ndikanakhalabe ndi chitonthozo ichi, ndikanakondwa mu ululu wanga wosalekezawu podziwa kuti sindinakane mawu a Woyerayo. “Kodi mphamvu zanga nʼzotani kuti ndizikhalabe ndi chiyembekezo? Nanga zoyembekezera zanga nʼzotani kuti ndipirirebe? Kodi ine ndili ndi mphamvu? Nanga thupi langa ndi lolimba ngati chitsulo? Kodi ndili ndi mphamvu zodzithandizira ndekha, nanga pakuti thandizo lachotsedwa kwa ine? “Munthu amene ali kakasi ayenera kukhala ndi abwenzi odzipereka, ngakhale kuti iyeyo wasiya kuopa Wamphamvuzonse. Koma abale anga ndi wosadalirika ngati mitsinje yowuma msanga, ngati mitsinje imene imathamanga. Ali ngati mitsinje ya madzi akuda nthawi ya dzinja, imene madzi ake amakhala ambiri chifukwa chakuchuluka kwa mvula, koma madziwo amasiya kuyenda nthawi yachilimwe, ndipo nthawi yotentha madziwo amawumiratu mʼmitsinjemo. Anthu oyenda pa ngamira amapatukirako kufuna madzi; iwo amangoyendayenda nʼkufera mʼchipululu. Anthu oyenda pa ngamira a ku Tema amafunafuna madzi, anthu amalonda apaulendo a ku Seba amafunafuna mwa chiyembekezo. Amataya mtima chifukwa ankayembekezera kupeza madzi; koma akafika kumeneko, amangokhumudwako. Tsono inunso mukuonetsa kuti ndinu osathandiza, mukuona chinthu choopsa kwambiri ndipo mukuchita mantha. Kodi ine ndinanenapo kuti, ‘Ndiperekereni kenakake, ndilipirireni dipo kuchokera pa chuma chanu, ndilanditseni mʼdzanja la mdani, ndiwomboleni mʼdzanja la munthu wankhanza?’ “Phunzitseni, ndipo ine ndidzakhala chete; ndionetseni pomwe ndalakwitsa. Ndithu, mawu owona ndi opweteka! Koma mawu anu otsutsa akufuna kuonetsa chiyani? Kodi inu mukufuna kundidzudzula pa zimene ndikunena, ndipo mukufuna kuyesa mawu a munthu wosweka mtima ngati mphepo chabe? Inu mungathe kuchita maere kuti mugulitse ana amasiye ndi kumugulitsa bwenzi lanu. “Koma tsopano ndichitireni chifundo pamene mukundiyangʼana. Kodi ine ndingayankhule zabodza pamaso panu? Fewani mtima, musachite zosalungama; ganiziraninso popeza chilungamo changa chikanalipobe. Kodi pali choyipa chilichonse pa milomo yanga? Kodi pakamwa panga sipangathe kuzindikira kanthu koyipa? “Kodi munthu sakhala ndi ntchito yowawa pa dziko lapansi? Kodi masiku ake sali ngati munthu waganyu? Monga ngati kapolo wolakalaka mthunzi wa nthawi yamadzulo, kapena ngati munthu waganyu woyembekezera malipiro ake, choncho ine ndapatsidwa nthawi yongovutika pachabe, ndiponso usiku wamasautso wapatsidwa kwa ine. Ndikamagona ndimaganiza kuti, ‘Kodi kucha liti?’ Usikuwo umatalika ndipo sindigona tulo mpaka mmawa. Thupi langa ladzala mphutsi ndi zipsera, khungu langa langʼambika ndipo likutuluka mafinya. “Masiku anga ndi othamanga kupambana makina wolukira nsalu, ndipo amatha wopanda chiyembekezo. Inu Mulungu kumbukirani kuti moyo wanga uli ngati mpweya; sindidzaonanso masiku achisangalalo. Amene akundiona tsopano akundiona; mudzandifunafuna koma sindidzapezekanso. Monga mtambo umazimirira ndi kukanganuka, momwemonso munthu amene walowa mʼmanda sabwerera. Iye sadzabweranso ku nyumba kwake ndipo onse omudziwa adzamuyiwala. “Nʼchifukwa chake ine sindidzakhala chete; ndidzayankhula mopsinjika mtima, ndidzadandaula mowawidwa mtima. Kodi ine ndine nyanja kapena chirombo chamʼnyanja kuti inu mundiyikire alonda? Pamene ndikuganiza kuti ndidzapeza chitonthozo pa bedi panga ndipo pogona panga padzachepetsa madandawulo anga, ngakhale nthawi imeneyo mumandiopseza ndi maloto ndi kundichititsa mantha ndi masomphenya, kotero kuti ndimalakalaka kudzikhweza kapena kufa, kupambana kupirira zowawa zimene ndikuzimva mʼthupi mwanga. Ine ndatopa nawo moyo wanga; sindingakonde kukhala moyo nthawi zonse. Ndisiyeni ndekha pakuti moyo wanga ulibe tanthauzo. “Kodi munthu nʼchiyani kuti muzimuganizira chotere, kuti muzisamala zochita zake, kuti muzimusanthula mmawa uliwonse ndi kumamuyesa nthawi yonse? Kodi simudzaleka kumandizonda kuti ndipezeko mpata wopumula? Ngati ine ndachimwa, ndachita chiyani kwa Inu, Inu wopenyetsetsa anthu? Chifukwa chiyani mwachititsa kuti ndikhale ngati choponyera chandamale chanu? Kodi ndasanduka katundu wolemera kwa Inu? Chifukwa chiyani simukundikhululukira zolakwa zanga ndi kundichotsera machimo anga? Pakuti posachedwa ndilowa mʼmanda; mudzandifunafuna ine koma simudzandionanso.” Mawu a Bilidadi Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti, “Kodi udzakhala ukuyankhula zoterezi mpaka liti? Mawu ako ali ngati mphepo yamkuntho. Kodi Mulungu amapotoza chiweruzo cholungama? Kodi Wamphamvuzonse amalephera kuchita zachilungamo? Pamene ana ako anamuchimwira Mulungu, Iye anawapereka kuti alangidwe chifukwa cha tchimo lawo. Koma utayangʼana kwa Mulungu, ndi kudandaulira Wamphamvuzonse, ngati uli wangwiro ndi wolungama mtima ngakhale tsopano Iye adzachitapo kanthu mʼmalo mwako ndipo adzakubwezeretsa pa malo ako oyenera. Chiyambi chako chidzaoneka ngati chochepa koma chimaliziro chako chidzakhala chopambana. “Funsa kwa anthu amvulazakale ndipo upeze zimene makolo awo anaziphunzira pakuti ife ndife ana adzulodzuloli ndipo sitidziwa chilichonse, ndipo moyo wathu pa dziko lapansi uli ngati chithunzithunzi. Kodi iwo sadzakulangiza ndi kukufotokozera? Kodi sadzakuwuza mawu ochokera pa zimene amazidziwa? Kodi bango nʼkumera pa nthaka yopanda chinyontho? Nanga mawango nʼkukula bwino popanda madzi? Popanda madzi, zimenezi zimafota zikanali zaziwisi ndi zosadula; zimawuma msangamsanga kuposa bango. Ndimo mmene amachitira anthu onse amene amayiwala Mulungu; ndi mmene chiyembekezo cha munthu wosapembedza Mulungu chimathera. Kulimba mtima kwake kumafowoka; zimene iye amadalira zili ngati ukonde wa kangawude. Iye amatsamira ukonde wake, koma umaduka; amawugwiritsitsa koma sulimba. Munthu woyipayo ali ngati chomera chothiriridwa bwino chimene chili pa dzuwa, nthambi zake zimatambalala pa munda wake; mizu yake imayanga pa mulu wa miyala ndi kufunafuna malo woti izikike pa miyalapo. Koma pamene yachotsedwa pamalo pakepo, pamalopo pamakana chomeracho ndi kuti, ‘Ine sindinakuonepo.’ Ndithudi chomeracho chimafota, ndipo pa nthakapo pamatuluka zomera zina. “Ndithudi, Mulungu sakana munthu amene alibe cholakwa kapena kulimbikitsa anthu ochita zoyipa. Iye adzadzaza mʼkamwa mwako ndi phwete ndipo milomo yako idzafuwula ndi chimwemwe. Adani ako adzachita manyazi, ndipo malo okhalamo anthu oyipa sadzaonekanso.” Mawu a Yobu Ndipo Yobu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikudziwa kuti zimenezi ndi zoona. Koma munthu angathe bwanji kukhala wolungama pamaso pa Mulungu? Ngakhale wina atafuna kutsutsana naye, Iye sangamuyankhe munthuyo ngakhale mawu amodzi omwe. Mulungu ndi wa nzeru zambiri ndipo mphamvu zake ndi zochuluka. Ndani analimbana naye popanda kupwetekeka? Iye amasuntha mapiri, mapiriwo osadziwa, ndipo amawagubuduza ali wokwiya. Iye amagwedeza dziko lapansi kulisuntha pamalo pake ndipo amanjenjemeretsa mizati yake. Iye amayankhula ndi dzuwa ndipo siliwala; Iyeyo amaphimba kuwala kwa nyenyezi. Ndi Mulungu yekha amene anayala mayiko akumwamba ndipo amayenda pa mafunde a pa nyanja. Iye ndiye mlengi wa nyenyezi zamlalangʼamba ndi akamwiniatsatana, nsangwe ndi kumpotosimpita. Iye amachita zozizwitsa zimene sizimvetsetseka, zodabwitsa zimene sizingawerengeke. Akapita pafupi ndi ine sindingathe kumuona; akadutsa, sindingathe kumuzindikira. Ngati Iye alanda zinthu, ndani angathe kumuletsa? Ndani anganene kwa Iye kuti, ‘Mukuchita chiyani?’ Mulungu sabweza mkwiyo wake; ngakhale gulu lankhondo la Rahabe linawerama pa mapazi ake. “Nanga ine ndingathe kukangana naye bwanji? Ndingawapeze kuti mawu oti nʼkutsutsana naye? Ngakhale nditakhala wosalakwa, sindingamuyankhe; ndikanangopempha chifundo kwa woweruza wanga. Ngakhale ndikanamuyitana ndipo Iye ndi kuvomera, sindikhulupirira kuti akanamva mawu angawo. Iye akanandikantha ndi mphepo yamkuntho, ndipo akanandipweteka popanda chifukwa. Mulungu sakanandilola kuti ndipumenso koma akanandichulukitsira zowawa. Tikanena za mphamvu, Iye ndi wamphamvudi! Ndipo tikanena za chiweruzo cholungama, ndani angamuzenge mlandu? Ngakhale ndikanakhala wosalakwa, zoyankhula zanga zikananditsutsa; ndikanakhala wopanda cholakwa, pakamwa panga pakanandipeza wolakwa. “Ngakhale ine ndili wosalakwa, sindidziyenereza ndekha; moyo wanga ndimawupeputsa. Zonse nʼzofanana; nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Iye amawononga anthu osalakwa ndi anthu oyipa omwe.’ Pamene mkwapulo ubweretsa imfa yadzidzidzi, Iye amaseka tsoka la munthu wosalakwayo. Pamene dziko lagwa mʼmanja mwa anthu oyipa Iye amawatseka maso anthu oweruza dzikolo. Ngati si Iyeyo, nanga ndani? “Masiku anga ndi othamanga kwambiri kupambana munthu waliwiro; masikuwo amapita ine osaonapo zabwino. Amayenda ngati mabwato a njedza pa nyanja, ngati mphungu zothamangira nyama zoti zidye. Nʼtanena kuti, ‘Ndidzayiwala madandawulo anga, ndidzasintha nkhope yanga ndipo ndidzasekerera,’ ndikuopabe mavuto anga onse, popeza ndikudziwa kuti simudzavomereza kuti ndine wosalakwa. Popeza ndapezeka kale wolakwa ndivutikirenji popanda phindu? Ngakhale nditasamba mʼmadzi oyera kwambiri ndi kusamba mʼmanja mwanga ndi sopo, mutha kundiponyabe pa dzala, kotero kuti ngakhale zovala zanga zomwe zidzandinyansa. “Mulungu si munthu ngati ine kuti ndithe kumuyankha, sindingathe kutsutsana naye mʼbwalo la milandu. Pakanapezeka munthu wina kuti akhale mʼkhalapakati wathu, kuti atibweretse ife tonse pamodzi, munthu wina woti achotse ndodo ya Mulungu pa ine kuti kuopsa kwake kusandichititsenso mantha! Pamenepo ine ndikanatha kuyankhula mosamuopa Mulunguyo, koma monga zililimu, sindingathe. “Ine ndatopa nawo moyo wanga; choncho ndidzanena zodandaula zanga momasuka ndipo ndidzayankhula mwa kuwawidwa mtima kwanga. Ndidzati kwa Mulungu wanga: Musandiweruze kuti ndine wolakwa, koma mundiwuze chifukwa chimene Inu mukukanganira ndi ine. Kodi mumakondwera mukamandizunza, kunyoza ntchito ya manja anu, chonsecho mukusekerera ndi zochita za anthu oyipa? Kodi maso anu ali ngati a munthu? Kodi mumaona zinthu monga momwe amazionera munthu? Kodi masiku anu ali ngati masiku a munthu, kapena zaka zanu ngati zaka za munthu, kuti Inu mufufuze zolakwa zanga ndi kulondola tchimo langa, ngakhale mukudziwa kuti sindine wolakwa ndiponso kuti palibe amene angandilanditse mʼdzanja lanu? “Munandiwumba ndi kundipanga ndi manja anu. Kodi tsopano Inu mudzatembenuka ndi kundiwononga? Kumbukirani kuti munandipanga ndi dothi, kodi tsopano mundibwezeranso ku fumbi? Suja munapatsa abambo anga mphamvu zoti andibale, suja munandikuza bwino mʼmimba mwa amayi anga? Munandikuta ndi khungu ndi mnofu ndi kundilumikiza pamodzi ndi mafupa ndi mitsempha? Munandipatsa moyo ndi kundionetsa chifundo chanu, ndipo munasamalira bwino moyo wanga. “Koma izi ndi zimene munabisa mu mtima mwanu, ndipo ndikudziwa kuti zinali mʼmaganizo anu: Kuti ngati ndingachimwe mudzakhala mukundipenyetsetsa ndipo kuti simudzalola kuti ndisalangidwe chifukwa cha kulakwa kwanga. Ngati ndili wolakwa, tsoka langa! Koma ngakhale ndili wosalakwa sindingathe kutukula mutu wanga, pakuti ndagwidwa ndi manyazi ndipo ndamizidwa mʼmavuto anga. Ndipo ndikatukula mutu wanga, Inu mumandisaka ngati mkango ndiponso mumandiopseza ndi mphamvu yanu. Mumabweretsa mboni zatsopano potsutsana nane ndipo mkwiyo wanu pa ine umanka nukulirakulira ndi magulu anu olimbana nane amanka nachulukirachulukira. “Chifukwa chiyani Inu munalola kuti ndibadwe? Ndi bwino ndikanafa diso lililonse lisanandione. Ndikanapanda kubadwa, kapena akanangonditenga nditabadwa kupita nane ku manda! Kodi masiku anga owerengeka sali pafupi kutha? Ndilekeni kuti ndipumule pangʼono pokha ndisanapite ku malo amene munthu sabwererako ku dziko la imfa ndi kwa mdima wandiweyani, ku dziko la mdima wandiweyani ndi chisokonezo, kumene kuwala kumakhala ngati mdima.” Mawu a Zofari Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti, “Kodi mawu ambirimbiriwa nʼkukhala osayankhidwa? Kodi munthu woyankhulayankhulayu nʼkulungamitsidwa? Kodi anthu nʼkukhala chete atamva kubwebweta kwakoku? Kodi palibe wina amene adzakudzudzule pamene ukuyankhula zonyoza? Iwe ukunena kwa Mulungu kuti, ‘Zikhulupiriro zanga ndi zopanda zolakwika ndipo ndine wangwiro pamaso panu.’ Aa, nʼkanakonda Mulungu akanayankhula kuti Iye atsekule pakamwa pake kutsutsana nawe ndi kukuwululira chinsinsi cha nzeru yake, pakuti nzeru yeniyeni ili ndi mbali ziwiri. Dziwa izi: Mulungu wayiwala machimo ako ena. “Kodi iwe ungathe kumvetsa zinsinsi za Mulungu? Kodi ungafufuze malire a nzeru za Wamphamvuzonse? Zili kutali kupambana mayiko akumwamba, nanga ungachite chiyani? Ndi zakuya kupambana kuya kwa manda, nanga ungadziwe chiyani? Muyeso wa nzeru zake ndi wautali kupambana dziko lapansi ndipo ndi wopingasa kupambana nyanja. “Ngati Iye atabwera ndi kukutsekera mʼndende nakutengera ku bwalo la milandu, ndani angathe kumuletsa? Ndithudi, Mulungu amazindikira anthu achinyengo; akaona choyipa, kodi sachizindikira? Munthu wopanda nzeru sizingatheke kukhala wanzeru monganso mwana wa bulu wakuthengo sangasanduke munthu. “Koma ngati upereka mtima wako kwa Iye ndi kutambasulira manja ako kwa Iyeyo, ngati utaya tchimo limene lili mʼdzanja lako ndi kusalola choyipa kuti chikhale mʼmoyo mwako, udzatukula mutu wako wosachita manyazi; udzayima chilili ndipo sudzachita mantha. Udzayiwala ndithu zowawa zako, zidzakhala ngati madzi amene apita kale. Moyo wako udzawala kupambana usana, ndipo mdima udzakhala ngati mmawa. Udzalimba mtima popeza pali chiyembekezo; ndipo udzayangʼana mbali zonse ndi kugona mosatekeseka. Udzagona pansi, popanda wina wokuopseza ndipo ambiri adzakupempha kuti uwachitire chifundo. Koma anthu oyipa adzafuna thandizo osalipeza, ndipo adzasowa njira yothawirapo; chiyembekezo chawo chidzakhala imfa basi.” Mawu a Yobu Pamenepo Yobu anayankha kuti, “Ndithudi inuyo ndinu anthu ndipo nzeru zanu zidzafera nanu pamodzi! Koma inenso ndili nazo nzeru ngati inu; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Ndani amene sadziwa zonse zimene mwanenazi? “Ndasanduka chinthu choseketsa kwa abwenzi anga, ngakhale ndinkapemphera kwa Mulungu ndipo Iye ankandiyankha. Ine ndasanduka chinthu chongoseketsa, ngakhale ndili wolungama ndi wosalakwa! Anthu amene ali pabwino amanyoza anzawo amene ali pa tsoka. Tsokalo limagwa pa amene wayamba kale kugwa. Nyumba za anthu achifwamba zimakhala pa mtendere, ndipo anthu amene amaputa Mulungu amakhala pabwino, amene amanyamula milungu yawo mʼmanja. “Koma funsa nyama zakuthengo ndipo zidzakuphunzitsa, kapena mbalame zamumlengalenga ndipo zidzakuwuza; kapena uyankhule ndi dziko lapansi ndipo lidzakuphunzitsa, kapena ulole nsomba zamʼnyanja kuti zikufotokozere. Kodi mwa zonsezi ndi chiti chimene sichidziwa kuti lachita zimenezi ndi dzanja la Yehova? Mʼmanja mwake ndi mʼmene muli moyo wa cholengedwa chilichonse, ndiponso moyo wa anthu a mitundu yonse. Kodi khutu sindiye limene limamva mawu monga mmene lilime limalawira chakudya? Kodi nzeru sipezeka pakati pa anthu okalamba? Kodi moyo wautali sumabweretsa nzeru zomvetsa zinthu? “Kwa Mulungu ndiye kuli nzeru ndi mphamvu; uphungu ndi kumvetsa zinthu ndi zake. Chimene Iye wapasula palibe angachimangenso. Akatsekera munthu mʼndende palibe angamutulutse. Iyeyo akamanga mvula dziko limawuma; akamasula mvulayo, madzi amasefukira pa dziko. Kwa Iye kuli mphamvu ndi kupambana; munthu wopusitsidwa ndiponso wopusitsa onse ali mu ulamuliro wake. Iye amalanda aphungu nzeru zawo ndipo amapusitsa oweruza. Iye amachotsa zingwe zimene mafumu anawamanga nazo ndipo amawamanga lamba mʼchiwuno mwawo. Iye amasocheretsa ansembe atawalanda nzeru zawo ndipo amagonjetsa anthu amphamvu amene ndi okhazikika. Iye amakhalitsa chete aphungu odalirika ndipo amalanda chidziwitso cha anthu akuluakulu. Iye amanyoza anthu otchuka ndipo anthu anyonga amawatha mphamvu. Iye amatulutsira poyera zinthu zozama za mu mdima ndipo mdima wandiweyaniwo amawusandutsa kuwala. Iye amakuza mitundu ya anthu ndipo amayiwononganso; amachulukitsa mitundu ya anthu ndipo amayimwazanso. Iye amalanda nzeru za atsogoleri a dziko lapansi; amawayendetsa mʼthengo mopanda njira. Iwo amafufuzafufuza njira mu mdima wopanda chowunikira; Iye amawayendetsa dzandidzandi ngati oledzera. “Ndaziona ndi maso anga zonsezi, ndazimva ndi makutu anga ndipo ndazimvetsa. Zimene inu mukudziwa, inenso ndimazidziwa; ineyo sindine munthu wamba kwa inu. Koma ine ndikulakalaka nditayankhula ndi Wamphamvuzonse ndi kukamba mlandu wanga ndi Mulungu. Koma inu mukundipaka mabodza; nonsenu ndinu asingʼanga opanda phindu! Achikhala munangokhala chete nonsenu! Apo mukanachita zanzeru. Tsopano imvani kudzikanira kwanga; imvani kudandaula kwa pakamwa panga. Kodi inu mudzayankhula moyipa kuyankhulira Mulungu? Kodi mudzayankhulira Iyeyo mwachinyengo? Kodi mudzaonetsa kuti Iyeyo ngokondera? Kodi inu mudzamuteteza Mulungu pa mlandu wake? Mulungu atayangʼanitsitsa, inu nʼkukupezani wosalakwa? Kodi inu mungamunamize Iye monga momwe munganamizire munthu? Ndithudi, Iye angathe kukudzudzulani ngati muchita zokondera mseri. Kodi ulemerero wake sungakuopseni? Kodi kuopsa kwake sikungakuchititseni mantha? Mawu anu anzeru ali ngati miyambi yopanda tanthauzo; mawu anu odzitchinjirizira ali ngati mpanda wadothi. “Khalani chete ndipo ndilekeni ndiyankhule; tsono zimene zindichitikire zichitike. Chifukwa chiyani ndikuyika moyo wanga pa chiswe ndi kutengera mʼmanja moyo wangawu? Ngakhale Iye andiphe, komabe ndidzamukhulupirira; ndithu, ndidzafotokoza mlandu wanga pamaso pake. Zoonadi, ichi ndiye chidzakhala chipulumutso changa pakuti palibe munthu wosapembedza amene angafike pamaso pake! Mvetserani mosamala mawu anga; makutu anu amve zimene ndikunena. Pakuti tsopano ndawukonzekera mlandu wanga, ndikudziwa ndipo adzandipeza wolungama. Kodi alipo wina amene angatsutsane nane? ngati zili choncho, ndidzakhala chete ndi kufa. “Inu Mulungu, ndipatseni zinthu ziwiri izi, ndipo pamenepo ine sindidzakubisalirani: Muchotse dzanja lanu pa ine, ndipo muleke kundichititsa mantha ndi kuopsa kwanuko. Tsono muyitane ndipo ndidzayankha, kapena mulole kuti ine ndiyankhule ndipo Inu muyankhe. Kodi zolakwa zanga ndi zingati ndipo machimo anga ndi angati? Wonetseni kulakwa kwanga ndi machimo anga. Chifukwa chiyani mukundifulatira ndi kundiyesa ine mdani wanu? Kodi mudzazunza tsamba lowuluka ndi mphepo? Kodi mudzathamangitsa mungu wowuma? Pakuti Inu mwalemba zinthu zowawa zonditsutsa nazo ndipo mukundipaka machimo a pa ubwana wanga. Inu mwamanga miyendo yanga ndi maunyolo. Mumayangʼanitsitsa mayendedwe anga onse poyika zizindikiro pamene mapazi anga apondapo. “Motero munthu amatha ngati chinthu chofumbwa, ngati chovala chodyedwa ndi njenjete. “Munthu wobadwa mwa amayi amakhala masiku owerengeka ndipo ndi odzaza ndi mavuto okhaokha. Amaphuka ngati duwa ndipo kenaka amafota; amathawa ngati mthunzi ndipo sakhalitsa. Kodi munthu wotereyo nʼkumuyangʼanitsitsa? Kodi mungamubweretse pamaso panu kuti mumuzenge mlandu? Ndani angatulutse chabwino mʼchoyipa? Palibe ndi mmodzi yemwe! Masiku a munthu ndi odziwikiratu; munakhazikitsa chiwerengero cha miyezi yake ndipo munamulembera malire amene sangathe kuwalumpha. Choncho Inu mumufulatire ndipo mumuleke apumule kufikira atakondwera nawo moyo ngati munthu waganyu. “Mtengo uli nacho chiyembekezo: ngati wadulidwa, udzaphukiranso ndipo nthambi zake sizidzaleka kuphukira. Mizu yake ingathe kukalamba mʼnthaka ndipo chitsa chake nʼkuwola pa dothi, koma pamene chinyontho chafika udzaphukira ndipo udzaphuka nthambi ngati mtengo wanthete. Koma munthu amafa nayikidwa mʼmanda, amapuma mpweya wotsiriza ndipo kutha kwake nʼkomweko. Monga madzi amaphwera mʼnyanja kapena monga mtsinje umaphwera nuwuma, momwemonso munthu amagona ndipo sadzukanso; mpaka zamlengalenga zidzathe, anthu sadzauka kapena kudzutsidwa ku tulo tawo. “Aa, Inu mukanangondibisa mʼmanda ndi kundiphimba kuti ndisaoneke mpaka mkwiyo wanu utapita! Achikhala munandiyikira nthawi, kuti pambuyo pake mundikumbukirenso. Munthu akafa, kodi adzakhalanso ndi moyo? Masiku anga onse a moyo wovutikawu ndidzadikira mpaka itafika nthawi yomasulidwa. Inu mudzandiyitane ndipo ndidzakuyankhani; inu mudzafunitsitsa kuona cholengedwa chimene munachipanga ndi manja anu. Ndithudi pamenepo mudzayangʼana mayendedwe anga koma simudzalondola tchimo langa. Zolakwa zanga zidzakulungidwa mʼthumba; inu mudzaphimba tchimo langa. “Koma monga phiri limakokolokera ndi kuswekasweka ndipo monga thanthwe limasunthira kuchoka pa malo ake, monganso madzi oyenda amaperesera miyala ndipo madzi othamanga amakokololera nthaka, momwemonso Inu mumawononga chiyembekezo cha munthu. Inu mumamugonjetsa kamodzinʼkamodzi ndipo munthuyo nʼkutheratu; Inu mumasintha maonekedwe a nkhope yake ndipo mumamutaya kutali. Ana ake akamalemekezedwa, iyeyo sazidziwa zimenezo; akamachititsidwa manyazi iye saziona zimenezo. Iye amangomva zowawa za mʼthupi lake ndipo amangodzilirira yekha mwini wakeyo.” Mawu a Elifazi Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti, “Kodi munthu wanzeru angayankhe ndi mawu achabechabe otere, kapena angakhutitse mimba yake ndi mphepo yotentha yochokera kummawa? Kodi angathe kutsutsa ndi mawu opanda pake, kapena kuyankhula mawu opanda phindu? Koma iwe ukuchepetsa zoopa Mulungu ndipo ukutchinga zodzikhuthulira kwa Mulungu. Tchimo lako ndiye likuyankhulitsa pakamwa pakopo; ndipo watengera mayankhulidwe a atambwali. Pakamwa pakopo ndiye pakukutsutsa osati pakamwa panga; milomo yakoyo ikukutsutsa. “Kodi ndiwe munthu woyamba kubadwa? Kodi unalengedwa mapiri asanalengedwe? Kodi unali mʼgulu la alangizi a Mulungu? Kodi ukudziyesa wanzeru ndiwe wekha? Kodi iwe umadziwa chiyani chimene ife sitichidziwa? Kodi iwe uli ndi chidziwitso chanji chimene ife tilibe? Anthu a imvi ndi okalamba ali mbali yathu, anthu amvulazakale kupambana abambo ako. Kodi mawu otonthoza mtima ochokera kwa Mulungu sakukukwanira, mawu oyankhula mofatsawa kwa iwe? Chifukwa chiyani ukupsa mtima, ndipo chifukwa chiyani ukutuzula maso ako, moti ukupsera mtima Mulungu ndi kuyankhula mawu otero pakamwa pako? “Kodi munthu nʼchiyani kuti nʼkukhala woyera mtima kapena wobadwa mwa amayi nʼchiyani kuti nʼkukhala wolungama mtima? Ngati Mulungu sakhulupirira ngakhale angelo ake, ngakhale zakumwamba sizoyera pamaso pake, nanga kuli bwanji munthu amene ndi wonyansa ndi wa njira zokhotakhota, amene kuchita zoyipa kuli ngati kumwa madzi. “Mvetsera kwa ine ndipo ndidzakufotokozera; ndilole ndikuwuze zimene ndaziona, zimene anandiphunzitsa anthu anzeru, sanandibisire kalikonse kamene anamva kuchokera kwa makolo awo. (Ndi kwa iwowa kumene dziko lino linaperekedwa pamene panalibe mlendo wokhala pakati pawo). Munthu woyipa amavutika ndi masautso masiku onse a moyo wake, munthu wankhanza adzavutika zaka zake zonse. Amamva mawu owopsa mʼmakutu mwake, pamene zonse zikuoneka ngati zili bwino, anthu achifwamba amamuthira nkhondo. Iye sakhulupirira kuti angathe kupulumuka ku mdima wa imfa; iyeyo ndi woyenera kuphedwa. Amangoyendayenda pali ponse kunka nafuna chakudya; amadziwa kuti tsiku la mdima lili pafupi. Masautso ndi nthumanzi zimamuchititsa mantha kwambiri; zimamugonjetsa iye monga imachitira mfumu yokonzekera kukathira nkhondo, chifukwa iye amatambasula dzanja lake kuyambana ndi Mulungu ndipo amadzitama yekha polimbana ndi Wamphamvuzonse. Amapita mwa mwano kukalimbana naye atanyamula chishango chochindikala ndi cholimba. “Ngakhale nkhope yake ndi yonenepa ndipo mʼchiwuno mwake muli mnofu wambiri, munthuyo adzakhala mʼmizinda yowonongeka ndi mʼnyumba zosayenera kukhalamo anthu, nyumba zimene zikugwa ndi kuwonongeka. Iye sadzalemeranso ndipo chuma chake sichidzakhalitsa, ngakhale minda yake sidzabala zipatso pa dziko lapansi. Iyeyo sadzapulumuka mu mdimamo; lawi lamoto lidzawumitsa nthambi zake, ndipo mpweya wochokera mʼkamwa mwa Mulungu udzamusesa. Asadzinyenge yekha podalira zinthu zachabechabe, pakuti pa mapeto pake sadzaphulapo kanthu. Iye adzalandira malipiro ake nthawi yake isanakwane, ndipo nthambi zake sizidzaphukanso. Iye adzakhala ngati mtengo wamphesa wopululidwa zipatso zake zisanapse, adzakhala ngati mtengo wa olivi umene wayoyola maluwa ake. Pakuti anthu osapembedza Mulungu adzakhala osabala ndipo moto udzapsereza nyumba za onse okonda ziphuphu. Iwo amalingalira zaupandu ndipo amachita zoyipa; mtima wawo umakonzekera zachinyengo.” Mawu a Yobu Pamenepo Yobu anayankha kuti, “Ndinamvapo zambiri monga zimenezi; nonsenu ndinu anthu osatha kutonthoza mtima mnzanu. Kodi mawu anu ochulukawo adzatha? Kodi chikukuvutani nʼchiyani kuti muzingoyankhula mawu otsutsawa? Inenso ndikanatha kuyankhula monga inu, inuyo mukanakhala monga ndilili inemu; Ine ndikanatha kuyankhula mawu omveka bwino kutsutsana nanu ndi kukupukusirani mutu wanga. Ndipo mawu a pakamwa panga akanakulimbikitsani; chitonthozo chochokera pa milomo yanga chikanachepetsa ululu wanu. “Koma ine ndikati ndiyankhule ululu wanga sukuchepa; ndipo ndikati ndikhale chete, ululu wanga sukuchokabe. Ndithudi, Inu Mulungu mwanditha mphamvu; mwawononga banja langa lonse. Inu mwandimanga ndipo kundimangako kwakhala umboni; kuwonda kwanga kwandiwukira ndipo kukuchita umboni wonditsutsa. Mulungu amabwera kwa ine mwankhanza ndipo amadana nane, amachita kulumira mano; mdani wanga amandituzulira maso. Anthu amatsekula pakamwa pawo kundikuwiza; amandimenya pa tsaya mwachipongwe ndipo amagwirizana polimbana nane. Mulungu wandipereka kwa anthu ochita zoyipa ndipo wandiponyera mʼmanja mwa anthu oyipa mtima. Ine ndinali pamtendere, koma Mulungu ananditswanya; anandigwira pa khosi ndi kundiphwanya. Iye anandisandutsa choponyera chandamale chake; anthu ake oponya mauta andizungulira. Mopanda kundimvera chisoni, Iye akulasa impsyo zanga ndipo akutayira pansi ndulu yanga. Akundivulaza kawirikawiri, akuthamangira pa ine monga munthu wankhondo. “Ndasokerera chiguduli pa thupi langa ndipo ndayika mphamvu zanga pa fumbi. Maso anga afiira ndi kulira, ndipo zikope zanga zatupa; komatu manja anga sanachite zachiwawa ndipo pemphero langa ndi lolungama. “Iwe dziko lapansi, usakwirire magazi anga; kulira kwanga kofuna thandizo kusalekeke! Ngakhale tsopano mboni yanga ili kumwamba; wonditchinjiriza pa mlandu wanga ali komweko. Wondipembedzera ndi bwenzi langa, pamene maso anga akukhuthula misozi kwa Mulungu; iye, mʼmalo mwanga, amamudandaulira Mulungu monga munthu amadandaulira bwenzi lake. “Pakuti sipapita zaka zambiri ndisanayende mʼnjira imene sindidzabwerera.” “Mtima wanga wasweka, masiku anga atha, manda akundidikira. Ndithudi, anthu ondiseka andizungulira; maso anga akupenyetsetsa mdani wanga. “Inu Mulungu, patseni chikole chimene mukufuna. Ndani wina amene adzandiperekera ine chikole? Inu mwatseka maganizo awo kuti asamvetse zinthu; choncho simudzawalola kuti apambane. Ngati munthu apereka mnzake chifukwa cha chuma, ana ake sadzaona mwayi. “Mulungu wandisandutsa chisudzo chochiseka aliyense, munthu amene anthu amalavulira malovu nkhope yake. Mʼmaso mwanga mwada ndi chisoni; ndawonda ndi mutu womwe. Anthu olungama akudabwa nazo zimenezi; anthu osachimwa akupsera mtima anthu osapembedza Mulungu. Komabe anthu olungama adzasunga njira zawo, ndipo anthu a makhalidwe abwino mphamvu zawo zidzanka zikuchuluka. “Tsono bwerani nonsenu, bwerezaninso mawu anuwo, sindidzapezapo munthu wanzeru pakati panupo. Masiku anga atha, zimene ndinakonza zalephereka, pamodzinso ndi zokhumba za mtima wanga. Anthu awa amasandutsa usiku kukhala usana, nthawi ya usiku iwo amati ‘kwatsala pangʼono kucha.’ Ngati nyumba imene ndikuyiyembekezera ndi manda, ngati ndiyala bedi langa mu mdima, ngati ndinena kwa dzenje la manda ‘ndinu abambo anga,’ ndiponso kwa mphutsi kuti, ‘ndinu amayi anga’ kapena ‘mlongo wanga,’ tsono chiyembekezo changa chili kuti? Ndani angaone populumukira panga? Ndithu sindidzakhalanso ndi chiyembekezo chilichonse, polowa mʼmanda, pamene ndidzatsikira ku fumbi.” Mawu a Bilidadi Pamenepo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti, “Kodi iwe Yobu utsiriza liti zoyankhula zakozi? Khala munthu wozindikira zinthu ndipo ukatero ife tidzayankhula. Chifukwa chiyani ukutiyesa ngati ngʼombe ndi kuoneka ngati opusa mʼmaso mwako? Iwe amene ukudzipweteka wekha ndi mkwiyo wako, kodi dziko lapansi lisanduke bwinja chifukwa cha iweyo? Kodi kapena thanthwe lisunthidwe kuchoka pa malo ake? “Nyale ya munthu woyipa yazimitsidwa; malawi a moto wake sakuwalanso. Kuwala kwa mʼnyumba mwake kwasanduka mdima; nyale ya pambali pake yazima. Mayendedwe ake amgugu azilala; fundo zake zomwe zamugwetsa. Mapazi ake amulowetsa mu ukonde ndipo akungoyendayenda mu ukondewo. Msampha wamkola mwendo; khwekhwe lamugwiritsitsa. Amutchera msampha pansi mobisika; atchera diwa pa njira yake. Zoopsa zikumuchititsa mantha kumbali zonse, zikutsatira mayendedwe ake onse. Mphamvu zake zatha chifukwa cha njala, tsoka likumudikira. Wagwidwa nthenda yoopsa thupi lonse; miyendo yake, manja ake, zonse zawola. Wachotsedwa mʼnyumba imene ankadalira, ndipo amukokera ku imfa, mfumu ya zoopsa zonse. Mʼnyumba mwake zonse zachotsedwamo; awazamo sulufule kuti aphe tizirombo ta matenda. Mizu yake ikuwuma pansi ndipo nthambi zake zikufota Sadzakumbukiridwanso pa dziko lapansi; sadzakhalanso ndi chinthu chomutchukitsa mʼdziko. Amuchotsa pa malo owala ndi kumuponya ku mdima, ndipo amupirikitsa pa dziko lonse. Iye alibe ana kapena zidzukulu pakati pa anthu ake, kulibe wotsala kumene iye ankakhala. Anthu akumadzulo adabwa kwambiri ndi tsoka lake; anthu akummawa agwidwa ndi mantha aakulu. Ndithudi, izi ndiye zimagwera munthu woyipa; amenewa ndiye mathero a munthu amene sadziwa Mulungu.” Mawu a Yobu Pamenepo Yobu anayankha kuti, “Kodi mudzakhala mukundizunza mpaka liti, ndi kundilasa ndi mawu anuwo? Inuyo mwandinyoza kwambiri; mwanditsutsa mopanda manyazi. Ngati ndi zoona kuti ine ndasochera, cholakwachotu nʼchanga. Ngati ndithudi mukudziyika nokha pamwamba panga, ndi kugwiritsa ntchito kunyozedwa kwanga polimbana nane, pamenepa dziwani kuti Mulungu wandilakwira ndipo wandizinga ukonde wake. “Ngakhale ndifuwule kuti, ‘Akundizunza!’ Palibe wondiyankha; ngakhale ndipemphe thandizo, palibe wondichitira zolungama. Mulungu wanditsekera njira yanga kotero sindingathe kudutsa; waphimba njira zanga ndi mdima. Iye wandilanda ulemu wanga ndipo wandivula chipewa chaufumu pamutu panga. Wandiphwanyaphwanya mbali zonse ndipo ndatheratu; Iye wazula chiyembekezo changa ngati mtengo. Wandikwiyira ndipo akundiyesa mmodzi mwa adani ake. Ankhondo ake akubwera kwa ine mwamphamvu, akonzekera zodzalimbana nane ndipo azungulira nyumba yanga. “Mulungu wandisiyanitsa ndi abale anga; wasandutsa odziwana nane kukhala achilendo kwa ine. Abale anga andithawa; abwenzi anga andiyiwala. Anthu odzacheza ku nyumba kwanga ndiponso antchito anga aakazi andisandutsa mlendo; ndasanduka mlendo mʼmaso mwawo. Ndikayitana wa ntchito wanga, iye sandiyankha, ngakhale ndikapempha ndi pakamwa panga sandichitira kanthu. Mpweya wanga umamunyansa mkazi wanga; ndine chinthu chonyansa kwa abale anga a mimba imodzi. Inde, ngakhale ana amandinyoza; akandiona amandinyodola. Anzanga onse apamtima amanyansidwa nane; iwo amene ndinkawakonda andiwukira. Ndangotsala khungu ndi mafupa okhaokha; ndapulumuka lokumbakumba. “Mvereni chisoni, inu abwenzi anga, mvereni chisoni, pakuti dzanja la Mulungu landikantha. Chifukwa chiyani mukundilondola ngati Mulungu? Kodi simunatope nalo thupi langa? “Aa, achikhala mawu anga analembedwa, achikhala analembedwa mʼbuku, akanalembedwa pa mwala ndi chitsulo, akanalembedwa pa thanthwe kuti sangathe kufufutidwa! Koma ndikudziwa kuti mpulumutsi wanga ali ndi moyo, ndipo pa nthawi yomaliza adzabwera kudzanditeteza. Ndipo khungu langa litatha nʼkuwonongeka, mʼthupi langa lomweli ndidzamuona Mulungu. Ine ndemwe ndidzamuona Iye ndi maso angawa, ineyo, osati wina ayi. Ndithu mtima wanga ukufunitsitsadi! “Koma inu mukuti, ‘Haa! Tingamuzunze bwanji, popeza kuti zonsezi zaoneka chifukwa cha iye yemweyo?’ Inu muyenera kuopa lupanga; pakuti mkwiyo wake umalangadi ndi lupanga; zikadzatero muzadziwa kuti chiweruzo chilipo ndithu.” Mawu a Zofari Pamenepo Zofari wa ku Naama anayankha kuti “Kuvutika kwa mʼmaganizo kwanga kwandifulumiza kuti ndiyankhe chifukwa ndasautsidwa kwambiri. Ndikumva kudzudzula kondinyoza, ndipo kumvetsetsa kwanga kwa zinthu kwandifulumiza kuti ndiyankhe. “Ndithudi iwe ukudziwa momwe zinthu zakhala zikuchitikira kuyambira kale, kuchoka nthawi imene munthu analengedwa pa dziko lapansi, kuti chisangalalo cha woyipa nʼchosachedwa kutha, chimwemwe cha wosapembedza Mulungu nʼchakanthawi kochepa. Ngakhale atamayenda mapewa ake ali mmwamba ndipo mutu wake uli nengʼaa, iye adzatheratu monga momwe imatayikira ndowe yake yomwe; iwo amene ankamuona adzati, ‘Kodi uje uja ali kuti?’ Adzazimirira ngati maloto ndipo sadzapezekanso, adzachotsedwa ngati masomphenya a usiku. Diso limene linamuona silidzamuonanso; sadzapezekanso pamalo pake. Ana ake adzabwezera zonse zimene iyeyo analanda anthu osauka; Mphamvu zaunyamata zimene zili mʼthupi mwake zidzagona naye limodzi mʼfumbi. “Ngakhale zoyipa zili zozuna mʼkamwa mwake ndipo amazibisa kunsi kwa lilime lake, ngakhale salola kuzilavula, ndipo amazisunga mʼkamwa mwake, koma chakudya chake chidzawawasa mʼmimba mwake; chidzasanduka ngati ndulu ya njoka mʼkati mwa iyeyo. Adzachisanza chuma chimene anachimeza; Mulungu adzachitulutsa mʼmimba mwa munthuyo. Iye adzayamwa ndulu ya njoka ndipo ululu wa mphiri udzamupha. Sadzasangalala ndi timitsinje, mitsinje yoyenda uchi ndi mafuta. Ayenera kubweza zimene anazigwirira ntchito osazidya; sadzasangalala ndi phindu la malonda ake. Pakuti iye anapondereza anthu osauka ndipo anawasiya wopanda thandizo; iyeyo analanda nyumba zimene sanamange. “Chifukwa choti umbombo wake sutha, sadzatha kusunga chilichonse chimene amakondwera nacho. Palibe chatsala kuti iye adye; chuma chake sichidzachedwa kutha. Ngakhale ndi munthu wachuma, mavuto adzamugwera; mavuto aakulu adzamugwera. Akadya nʼkukhuta, Mulungu adzamugwetsera ukali wamoto ngati mvula yosalekeza. Ngakhale athawe mkondo wachitsulo, muvi wamkuwa wosongoka udzamulasa. Muviwo adzawutulutsira ku msana, songa yake yowala kuchoka mʼmphafa mwake. Adzagwidwa ndi mantha aakulu; mdima wandiweyani ukudikira chuma chake. Moto wopanda wowukoleza udzamupsereza ndi kuwononga zonse zotsala mʼnyumba yake. Zamumlengalenga zidzawulula kulakwa kwake; dziko lapansi lidzamuwukira. Chigumula cha madzi chidzawononga nyumba yake, katundu wake adzatengedwa pa tsiku la ukali wa Mulungu. Izi ndi zimene Mulungu amasungira anthu oyipa, mphotho imene Mulungu amayikira iwowo.” Mawu a Yobu Pamenepo Yobu anayankha kuti, “Mvetserani bwino mawu anga; ichi chikhale chitonthozo changa chochokera kwa inu. Ndiloleni ndiyankhule ndipo ndikatha kuyankhula munditonzetonze. “Kodi ine ndikudandaulira munthu? Tsono ndilekerenji kupsa mtima? Ndipenyeni ndipo mudabwe; mugwire dzanja pakamwa. Ndikamaganiza zimenezi ndimachita mantha kwambiri; thupi langa limanjenjemera. Chifukwa chiyani anthu oyipa amakhalabe ndi moyo, amakalamba ndi kusanduka amphamvu? Amaona ana awo akukhazikika pamodzi nawo, zidzukulu zawo zikukula bwino iwo akuona. Mabanja awo amakhala pa mtendere ndipo sakhala ndi mantha; mkwapulo wa Mulungu suwakhudza nʼkomwe. Ngʼombe zawo zazimuna sizilephera kubereketsa; ngʼombe zawo zazikazi sizipoloza. Amatulutsa ana awo ngati gulu la nkhosa; makanda awo amavinavina pabwalo. Amayimba nyimbo pogwiritsa ntchito matambolini ndi azeze; amakondwa pakumva kulira kwa chitoliro. Zaka zawo zimatha ali mu ulemerero ndipo amatsikira ku manda mwamtendere. Koma anthuwo amawuza Mulungu kuti, ‘Tichokereni!’ Ife tilibe chikhumbokhumbo chofuna kudziwa njira zanu. Kodi Wamphamvuzonseyo ndani kuti timutumikire? Ife tipindula chiyani tikamapemphera kwa Iyeyo? Komatu ulemerero wawo suli mʼmanja mwawo, koma ine ndimakhala patali ndi uphungu wa anthu oyipa. “Koma nʼkangati kamene nyale ya anthu oyipa imazimitsidwa? Nʼkangati kamene tsoka limawagwera? Nʼkangati kamene Mulungu amawakwiyira ndi kuwalanga? Nʼkangati kamene iwo amakhala ngati phesi lowuluka ndi mphepo, ngati mungu wowuluzika ndi kamvuluvulu? Paja amati, ‘Mulungu amalanga ana chifukwa cha machimo abambo awo.’ Koma Mulungu amabwezera chilango munthuyo, kuti adziwe kuti Mulungu amalangadi. Mulole kuti adzionere yekha chilango chake, kuti alawe ukali wa Wamphamvuzonse. Nanga kodi amalabadira chiyani zabanja lake limene walisiya mʼmbuyo, pamene chiwerengero cha masiku ake chatha? “Kodi alipo wina amene angaphunzitse Mulungu nzeru, poti Iye amaweruza ngakhale anthu apamwamba? Munthu wina amamwalira ali ndi mphamvu zonse, ali pa mtendere ndi pa mpumulo, thupi lake lili lonenepa, mafupa ake ali odzaza ndi mafuta. Munthu wina amamwalira ali wowawidwa mtima, wosalawapo chinthu chabwino chilichonse. Olemera ndi osauka omwe amamwalira ndi kuyikidwa mʼmanda ndipo onse amatuluka mphutsi. “Ndikudziwa bwino zimene mukuganiza, ziwembu zanu zomwe mukuti mundichitire. Inu mukuti, ‘Kodi nyumba ya mkulu uja ili kuti, matenti amene munkakhala anthu oyipa aja ali kuti?’ Kodi munawafunsapo anthu amene ali pa ulendo? Kodi munaganizirapo zimene iwo amanena? Zakuti munthu woyipa amasungidwa chifukwa cha tsiku la tsoka, kuti amapulumutsidwa chifukwa cha tsiku la ukali wa Mulungu? Kodi ndani amadzudzula munthu wochimwayo? Ndani amamubwezera zoyipa zimene anachita? Iye amanyamulidwa kupita ku manda ndipo anthu amachezera pa manda ake. Dothi la ku chigwa limamukomera; anthu onse amatsatira mtembo wake, ndipo anthu osawerengeka amakhala patsogolo pa chitanda chakecho. “Nanga inu mudzanditonthoza bwanji ine ndi mawu anu opandapakewo palibe chimene chatsala kuti muyankhe koma mabodza basi!” Mawu a Elifazi Pamenepo Elifazi wa ku Temani anayankha kuti, “Kodi munthu nʼkukhala waphindu kwa Mulungu? Kodi munthu wanzeru angamupindulire Iye? Kodi Wamphamvuzonse akanapeza chabwino chotani iweyo ukanakhala wolungama? Kodi iyeyo akanapeza phindu lanji makhalidwe ako akanakhala angwiro? “Kodi nʼchifukwa choti umamuopa, kuti azikudzudzula, kuti azifuna kukukokera ku mlandu? Kodi osati nʼchifukwa chakuti kuyipa kwako nʼkwakukulu? Kodi machimo ako si opanda malire? Iwe unkawumiriza abale ako kuti akupatse chikole popanda chifukwa; umalanda anthu zovala zawo ndi kuwasiya amaliseche. Sunawapatse madzi anthu otopa, ndipo unawamana chakudya anthu anjala, ngakhale unali munthu wamphamvu, wokhala ndi malo akeake, munthu waulemu wake, wokhala mʼdzikomo. Ndipo akazi amasiye unawachotsa wopanda kanthu, ndipo unapondereza ana amasiye. Nʼchifukwa chake misampha yakuzungulira, nʼchifukwa chake tsoka ladzidzidzi lakuchititsa mantha, nʼchifukwa chake kuli mdima kuti sungathe kuona kanthu, nʼchifukwa chakenso madzi achigumula akumiza. “Kodi Mulungu sali kutalitali kumwamba? Ndipo ona nyenyezi zili mmwamba kwambirizo, ona kutalika kwake pamene zililipo! Komabe iweyo ukunena kuti, ‘Kodi Mulungu amadziwa chiyani? Kodi Iye amaweruza mu mdima woterewu? Mitambo yakuda yamuphimba, kotero kuti Iye sakutiona pamene akuyendayenda pamwamba pa thambopo.’ Kodi iwe udzayendabe mʼnjira yakale imene anthu oyipa ankayendamo? Iwo anachotsedwa nthawi yawo isanakwane, maziko awo anakokoloka ndi madzi achigumula. Anthuwo anati kwa Mulungu, ‘Tichokereni! Kodi Wamphamvuzonse angatichitire chiyani?’ Chonsecho ndi Iye amene anadzaza nyumba zawo ndi zinthu zabwino, choncho ine sindigwirizana ndi uphungu wa anthu oyipa. “Anthu olungama amaona kuwonongeka kwawo ndipo amakondwera; anthu osalakwa amangoseka, akamuona woyipa akulangidwa. Amanena kuti, ‘Ndithudi adani athu awonongeka ndipo moto wawononga chuma chawo!’ “Gonjera Mulungu kuti ukhale naye pamtendere; ukatero udzaona zabwino. Landira malangizo a pakamwa pake ndipo usunge mawu ake mu mtima mwako. Ukabwerera kwa Wamphamvuzonse udzabwezeretsedwa; ukachotsa zoyipa zonse zimene zimachitika mʼnyumba mwako, ndipo chuma chamtengowapatali nuchiona ngati fumbi, golide wa ku Ofiri numutaya ku miyala ya ku zigwa. Pamenepo Wamphamvuzonseyo adzakhala golide wako, siliva wako wamtengowapatali. Pamenepo udzakondwera naye Wamphamvuzonse ndipo udzakweza nkhope yako kwa Mulungu. Udzamupempha ndipo adzakumvera, ndipo udzapereka zimene unalonjeza. Chimene watsimikiza kuti uchite, chidzachitikadi, kuwala kudzakuwunikira pa njira yako. Pamene anthu agwetsedwa pansi, iwe nʼkunena kuti, ‘Akwezeni!’ Pamenepo Iye adzapulumutsa anthu oponderezedwa. Iye adzapulumutsa ngakhale munthu amene ndi wolakwa, ameneyo adzapulumutsidwa kudzera mʼkulungama kwako.” Yobu Pamenepo Yobu anayankha kuti, “Leronso kudandaula kwanga nʼkwakukulu kwambiri; Iye akundilanga kwambiri ngakhale ndi kubuwula. Ndikanangodziwa kumene ndikanamupeza Mulungu; ndikanangopita kumene amakhalako! Ndikanafotokoza mlandu wanga pamaso pake ndipo ndikanayankhula mawu odziteteza. Ndikanadziwa mawu amene Iye akanandiyankha, ndi kulingalira bwino zimene akananena! Kodi Iye akanalimbana nane mwa mphamvu zake zazikulu? Ayi, Iye sakanayankhula zinthu zotsutsana nane. Kumeneko munthu wolungama akanafotokoza mlandu wake pamaso pake, ndipo woweruzayo akanandipeza wosalakwa nthawi zonse. “Taonani, ndikapita kummawa, Iye kulibe kumeneko, ndikapita kumadzulo sinditha kumupeza kumeneko. Akamagwira ntchito kumpoto, sindimuona kumeneko akapita kummwera, sindimuona. Koma Iye amadziwa mmene ndimayendera; Iyeyo akandiyesa adzandipeza kuti ndili ngati golide. Mapazi anga akhala akuponda mʼmapazi ake; ndasunga njira yake ndipo sindinayitaye. Sindinapatuke kusiya malamulo ochokera pakamwa pake; ndasunga mawu a pakamwa pake kupambana chakudya changa cha tsiku ndi tsiku. “Koma Iyeyo ndi wosasinthika, ndipo ndani angatsutsane naye? Iye amachita chilichonse chimene wafuna. Iye amachita chimene watsimikiza kuti chindichitikire, ndipo malingaliro oterowa ali nawobe. Nʼchifukwa chake ndikuchita mantha kwambiri pamaso pake; ndikamaganiza zonsezi ndimamuopa. Mulungu walefula mtima wanga; Wamphamvuzonse wandiopseza kwambiri. Komatu sindinachititsidwe mantha ndi mdima, ndi mdima wandiweyani umene waphimba nkhope yanga. “Chifukwa chiyani Wamphamvuzonse sayikiratu nthawi yoti aweruze? Chifukwa chiyani iwo amene amadziwa Iyeyo amayembekezera pachabe masiku oterewa? Anthu amasuntha miyala ya mʼmalire, kuti akuze dziko lawo; amadyetsa ziweto zimene aba. Amalanda abulu a ana amasiye ndipo amatenganso ngʼombe ya mkazi wamasiye ngati chikole. Amachotsa mʼmisewu anthu osauka, ndipo amathamangitsa amphawi onse mʼdziko. Amphawiwo amakhala ngati mbidzi mʼchipululu, amayendayenda kufuna chakudya; dziko lowuma limapereka chakudya cha ana awo. Iwo amakolola za mʼminda ya eni ake, ndipo amakunkha mphesa mʼminda ya anthu oyipa. Amagona maliseche usiku wonse kusowa zovala; pa nthawi yozizira amasowa chofunda. Amavumbwa ndi mvula ya mʼmapiri ndipo amakangamira ku matanthwe kusowa pobisalapo. Amatsomphola mwana wamasiye wa ku bere; ndipo amagwira mwana wakhanda wa mʼmphawi kuti akhale chikole. Amphawi amangoyenda maliseche kusowa zovala; amasenza mitolo ya tirigu, koma nʼkumagonabe ndi njala. Iwo amayenga mafuta a olivi mʼminda ya anthu oyipa; amapsinya mphesa, koma nʼkumamvabe ludzu. Kubuwula kwa anthu amene akufa kumamveka kuchokera mu mzinda, anthu ovulala akulirira chithandizo. Koma Mulungu sakuyimba mlandu wina aliyense. “Pali ena amene amakana kuwala, amene safuna kuyenda mʼkuwalako kapena kukhala mʼnjira zake. Dzuwa likalowa, wopha anzake amadzuka ndipo amakapha osauka ndi amphawi; nthawi ya usiku iye amasanduka mbala. Munthu wachigololo amadikira chisisira; iyeyo amaganiza kuti, ‘Palibe amene akundiona,’ ndipo amaphimba nkhope yake. Mbala zimathyola nyumba usiku, koma masana zimadzitsekera; izo zimathawa kuwala. Pakuti kwa onsewa mdima wandiweyani ndiye kuti kwawachera. Iwo amachita ubale ndi zoopsa za mdima. “Komatu iwowo ndi thovu loyandama pa madzi; minda yawo ndi yotembereredwa pa dzikolo kotero kuti palibe amene amapita ku minda ya mpesa. Monga momwe kutentha ndi chilala zimasungunulira madzi owundana ndi momwemonso mmene manda amachotsera omwe achimwa. Mayi wowabereka amawayiwala, mphutsi zimasangalala powadya; anthu oyipa sakumbukiridwanso koma amathyoka ngati mtengo. Amachitira nkhanza mayi wosabala ndi mayi amene alibe mwana, ndipo sakomera mtima mkazi wamasiye. Koma Mulungu amawononga munthu wamphamvu mwa mphamvu zake; ngakhale munthuyo atakhazikika, alibe chiyembekezo cha moyo wake. Mulungu atha kuwalola kuti akhale mosatekeseka, koma amakhala akupenyetsetsa njira zawo. Kwa kanthawi kochepa oyipa amakwezedwa ndipo kenaka saonekanso; amatsitsidwa ndipo amachotsedwa monga ena onse; amadulidwa ngati ngala za tirigu. “Ngati zimenezi sizoona, ndani angaonetse kuti ndine wabodza ndi kusandutsa mawu anga kukhala wopanda pake?” Mawu a Bilidadi Apo Bilidadi wa ku Suki anayankha kuti, “Ulamuliro ndi kuopsa ndi za Mulungu, Iye amakhazikitsa bata mu ufumu wake kumwambako. Kodi magulu ake ankhondo nʼkuwerengeka? Kodi kuwala kwake sikuwalira ndani? Kodi munthu angakhale bwanji wolungama pamaso pa Mulungu? Kodi munthu wobadwa mwa mayi angakhale wangwiro? Ngati mwezi sutha kuwala kwenikweni, ndipo nyenyezi sizitha kuwala pamaso pake, nanji tsono munthu amene ali ngati mphutsi, mwana wa munthu amene ali ngati nyongolotsi!” Mawu a Yobu Pamenepo Yobu anayankha kuti, “Wamuthandizadi munthu wopanda mphamvu! Walimbitsadi dzanja la munthu wofowoka! Wapereka malangizo kwa munthu amene alibe nzeru! Ndipotu waonetsadi nzeru zochuluka! Kodi wakuthandiza ndani kuti uyankhule mawu awa? Ndipo ndi mzimu wa yani umene unayankhula pakamwa pako? “Mizimu ya anthu akufa ikunjenjemera pansi pa madzi, ndi zonse zokhala mʼmadzimo. Dziko la anthu akufa ndi lapululu pamaso pa Mulungu; chiwonongeko ndi chosaphimbidwa. Mulungu anayala thambo la kumpoto pa phompho; Iye anakoloweka dziko lapansi mʼmalo mwake pamene panali popanda nʼkanthu komwe. Amasunga madzi ambiri mʼmitambo yake, koma mitamboyo siphulika chifukwa cha kulemera kwa madziwo. Iye amaphimba mwezi wowala, amawuphimba ndi mitambo yake. Mulungu anawalembera madzi malire wonga uta, kukhala malire pakati pa kuwunika ndi mdima. Mizati yochirikiza mitambo yakumwamba imanjenjemera, ndi kudabwa pa kudzudzula kwake. Ndi mphamvu zake anatontholetsa nyanja; ndi nzeru zake anakantha chirombo cha mʼmadzi chija chotchedwa Rahabe. Ndi mpweya wake anayeretsa zamumlengalenga, dzanja lake linapha chinjoka chothawa chija. Zimenezi ndi pangʼono chabe mwa ntchito yake; tingomva pangʼono za Iye ngati kunongʼona! Kodi ndani angathe kudziwa kukula kwa mphamvu zake?” Ndipo Yobu anapitiriza kuyankhula kwake: “Ndithu pali Mulungu wamoyo, amene wakana kundiweruza molungama, Wamphamvuzonse, amene wawawitsa mtima wanga, nthawi zonse pamene ndili ndi moyo, mpweya wa Mulungu uli mʼmphuno mwanga, pakamwa panga sipadzatuluka mawu oyipa, lilime langa silidzayankhula zachinyengo. Sindidzavomereza kuti inu mukunena zoona; mpaka imfa yanga, sindidzataya ungwiro wanga. Ndidzasunga chilungamo changa ndipo sindidzalola kuti chindichokere; chikumbumtima changa sichidzanditsutsa nthawi yonse ya moyo wanga. “Mdani wanga akhale ngati woyipa, wondiwukira akhale ngati munthu wosalungama! Nanga chiyembekezo cha munthu wosapembedza nʼchiyani pamene aphedwa, pamene Mulungu achotsa moyo wake? Kodi Mulungu amamva kulira kwake pamene zovuta zamugwera? Kodi adzapeza chikondwerero mwa Wamphamvuzonse? Kodi adzapemphera kwa Mulungu nthawi zonse? “Ndidzakuphunzitsani za mphamvu ya Mulungu ndipo sindidzabisa njira za Wamphamvuzonse. Inu mwadzionera nokha zonsezi. Nanga bwanji mukuyankhula zopanda pake? “Pano pali chilango chimene Mulungu amasungira woyipa, cholowa chimene munthu wankhanza amalandira kuchokera kwa Wamphamvuzonse. Angakhale ana ake achuluke chotani adzaphedwa ndi lupanga ndipo zidzukulu zake zidzasowa zakudya. Amene adzatsalireko adzafa ndi mliri, ndipo akazi awo amasiye sadzawalira. Ngakhale aunjike siliva ngati fumbi, ndi kukundika zovala ngati mchenga, zimene wasungazo wolungama ndiye adzavale, ndipo anthu osalakwa ndiwo adzagawane siliva wakeyo. Nyumba imene akuyimanga ili ngati mokhala kadziwotche, ili ngati msasa umene mlonda amamanga. Amapita kokagona ali wolemera koma kutha kwake nʼkomweko; akatsekula maso ake, chuma chake chonse chapita. Zoopsa zimamukokolola ngati madzi achigumula; mphepo yamkuntho imamunyamula usiku. Mphepo ya kummawa imamuwulutsa ndipo iye saonekanso ndipo imamuchotsa pamalo pake. Imakuntha pa iye osamuchitira chisoni, pamene akuyesa kuthawa mphamvu zake mwaliwiro. Mphepoyo imamuwomba ndithu ndipo kuchokera pamalo pake imamuopseza.” Pali mgodi wa siliva ndiponso malo oyengerapo golide. Chitsulo amachikumba pansi, ndipo mkuwa amawusungunula ku miyala yamkuwa. Munthu amalowa mu mdima atatenga nyale, amafunafuna miyala mpaka ku malire a mgodiwo, kufuna mkuwa mu mdima wandiweyani. Amakumba njira zapansi mu mgodimo, kutali ndi kumene kumakhala anthu, kumalo kumene phazi la munthu silinapondeko; iye amakhala ali lende pansipo namazungulira uku ndi uku. Nthaka, imene imatulutsa zakudya, kunsi kwake kumachita ngati kwasandulizika ndi moto; miyala ya safiro imachokera mʼmatanthwe ake, ndipo mʼfumbi lake mumakhala miyala yagolide. Palibe mbalame yodya zinzake imene imadziwa njira yobisikayi, palibe kamtema amene anayiona. Zirombo zolusa sizipondamo mʼnjiramo, ndipo mkango sudzeranso mʼmenemo. Munthu amaphwanya matanthwe olimba, ndipo amagubuduza mapiri kuyambira mʼtsinde. Amabowola njira mʼmatanthwewo; ndipo amaona chuma chonse cha mʼphirimo. Amaletsa mitsinje ya pansipo kuti isayendenso, motero amatulutsira poyera zinthu zobisika. “Koma nzeru zingapezeke kuti? Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti? Munthu sadziwa kufunika kwake kwa nzeruzo; nzeruyo sipezeka pa dziko lino la anthu amoyo. Phompho likuti, ‘Sizipezeka mwa ine muno.’ Nyanja ikuti, ‘Mwa ine munonso ayi.’ Nzeru sungazigule ndi golide wabwino kwambiri, mtengo wake sungawuyerekeze ndi siliva wambiri. Nzeru singagulidwe ndi golide wa ku Ofiri, kapena ndi miyala ya onikisi kapena ya safiro. Nzeru sungayiyerekeze ndi golide kapena mwala wa galasi, sungayigule ndi zokometsera zagolide. Miyala ya korali ndi krisitali siyoyeneranso ndi kuyitchula nʼkomwe; mtengo wa nzeru ndi woposa miyala ya rubi. Nzeru sungayiyerekeze ndi miyala ya topazi ya ku Kusi; nzeru singagulidwe ndi golide wabwino kwambiri. “Kodi tsono nzeru zimachokera kuti? Kodi kumvetsa zinthu kumakhala kuti? Malo ake ndi obisika kwa zamoyo zonse, ndi obisika ngakhale kwa mbalame zamlengalenga. Chiwonongeko ndi imfa zikuti, ‘Tangomva mphekesera chabe ya zimenezo!’ Mulungu yekha ndiye amadziwa njira yake yopita kumeneko, ndipo Iye yekha amadziwa kumene nzeru imakhala, pakuti Iye amayangʼana mpaka ku malekezero a dziko lapansi ndipo amaona zonse za kunsi kwa thambo. Iye atapatsa mphepo mphamvu zake, nayeza kuzama kwa nyanja, atakhazikitsa lamulo loti mvula izigwa ndi kukonza njira ya chingʼaningʼani cha bingu, pamenepo ndi pamene anayangʼana nzeruzo naziyeza mtengo wake; nazikhazikitsa ndi kuzisanthula bwino lomwe. Ndipo Iye anati kwa munthu, ‘Taonani, kuopa Ambuye, ndiye nzeru zimenezo ndipo kuthawa zoyipa ndiye kumvetsa zinthu kumeneko.’ ” Yobu anapitiriza kuyankhula kwake: “Aa! Ndikanakhala momwe ndinalili miyezi yapitayi, masiku amene Mulungu ankandiyangʼanira, pamene nyale yake inkandiwunikira ndipo ndi kuwunika kwakeko ine ndinkatha kuyenda mu mdima! Ndithu, masiku amene ndinali pabwino kwambiri, pamene ubwenzi wa Mulungu unkabweretsa madalitso pa nyumba yanga, nthawi imene Wamphamvuzonse anali nane, ndipo ana anga anali atandizungulira mʼmbalimu, pamene popondapo ine panali patakhathamira mafuta a mkaka, ndipo pa thanthwe pamatuluka mitsinje ya mafuta a olivi. “Pamene ndinkapita pa chipata cha mzinda ndi kukhala pa mpando wanga pabwalo, anyamata amati akandiona ankapatuka ndipo anthu akuluakulu ankayimirira; atsogoleri ankakhala chete ndipo ankagwira pakamwa pawo; anthu otchuka ankangoti duu, ndipo malilime awo anali atamatirira ku nkhama zawo. Aliyense amene anamva za ine anayankhula zabwino zanga, ndipo iwo amene anandiona ankandiyamikira, chifukwa ndinkapulumutsa mʼmphawi wofuna chithandizo, ndiponso mwana wamasiye amene analibe aliyense womuthandiza. Munthu amene anali pafupi kufa ankandidalitsa; ndinkasangalatsanso mkazi wamasiye. Chilungamo chinali ngati chovala changa; chiweruzo cholungama ndiye chinali mkanjo ndi nduwira yanga. Ndinali ngati maso kwa anthu osapenya; ndinali ngati mapazi kwa anthu olumala. Ndinali ngati abambo kwa anthu aumphawi; ndinkayimira mlendo pa mlandu wake. Ndinkawononga mphamvu za anthu oyipa ndi kulanditsa amene anali atagwidwa. “Ndinkaganiza kuti, ‘Ndidzafera mʼnyumba yanga, masiku a moyo wanga ali ochuluka ngati mchenga. Mizu yanga idzatambalalira ku madzi, ndipo mame adzakhala pa nthambi zanga usiku wonse. Ulemerero wanga udzakhala wosaguga mwa ine, ndipo uta wanga udzakhala watsopano nthawi zonse mʼdzanja langa.’ “Anthu ankamvetsera zimene ndinkanena mwachidwi, ankadikira atakhala chete kuti amve malangizo anga. Ndikayankhula, iwo sankayankhulanso; mawu anga ankawagwira mtima. Ankayembekezera ine monga momwe amayembekezera mvula ndipo ankalandira mawu anga ngati mvula ya mʼmalimwe. Ndikawasekerera, iwo sankatha kukhulupirira; kuwala kwa nkhope yanga chinali chinthu chamtengowapatali kwa iwowo. Ndinkawasankhira njira yawo ndipo ndinkawatsogolera ngati mfumu; ndinkakhala ngati mfumu pakati pa gulu lake lankhondo; ndinali ngati msangalatsi pakati pa anthu olira.” “Koma tsopano akundinyoza, ana angʼonoangʼono kwa ine, anthu amene makolo awo sindikanawalola kuti azithandizana ndi agalu anga kuweta nkhosa zanga. Kodi mphamvu zawo ndi za phindu lanji kwa ine, pakuti mphamvu zawo zinatha kale? Anali atatheratu kuwonda ndi njala, ankayendayenda mʼdziko lopanda madzi, mʼchipululu usiku. Ankathyola therere ndi masamba owawa, ndipo chakudya chawo chinali mizu ya mitengo ya masache. Anapirikitsidwa pakati pa anthu anzawo, akuwakuwiza ngati kuti anali akuba. Anawumirizidwa kukhala ku zigwembe za mitsinje yowuma, pakati pa matanthwe ndi mʼmaenje a mʼnthaka. Ankalira ngati nyama kuthengo ndipo ankawunjikana pamodzi pa ziyangoyango. Anali anthu achabechabe ndi wopanda dzina, anathamangitsidwa mʼdziko. “Ndipo tsopano ana awo akundiyimba nyimbo zachipongwe; ineyo ndasanduka chisudzo chawo. Iwo amanyansidwa nane ndipo amandithawa; akandiona salephera kundilavulira mʼmaso mwangamu. Tsopano pakuti Mulungu wakhwefula uta wanga ndipo wandisautsa, iwowo analekeratu kundiopa. Ku dzanja langa lamanja anthu akulimbana nane; andikumbira dzenje loti ndigweremo ndikamayenda, andipangira mitumbira ya nkhondo kuti alimbane nane. Iwo anditsekera njira; akufuna kundichititsa ngozi, popanda wina aliyense wowaletsa. Akundithamangitsa ngati madzi olowera pa mpanda wobowoka, iwo akubwererabwerera pakati pa chipasupasu. Zoopsa zandithetsa mphamvu; ulemu wanga wachita ngati wauluzika ndi mphepo, chuma changa chija chazimirira ngati mtambo. “Ndipo tsopano mtima wanga wachokamo; ndili mʼmasiku amasautso. Mafupa anga akuphwanya usiku pakuti zowawa zanga sizikuleka. Mʼmphamvu zake Mulungu wakhala ngati chovala changa; Iye wandigwira ngati chovala chondithina pa khosi. Wandiponya mʼmatope, ndipo ndasanduka ngati fumbi ndi phulusa. “Inu Mulungu, ine ndikulirira kwa Inu, koma simukundiyankha; ndikayimirira, Inu simundiyangʼana nʼkomwe. Inuyo mumandichitira zankhanza; mumandizunza ndi dzanja lanu lamphamvu. Mwandinyamulira ku mphepo ndipo mwandiwulutsa ndi mphepoyo; mwandiponya mʼmphepo ya mkuntho. Ndikudziwa kuti Inu mudzandifikitsa ku imfa, kumalo kumene amoyo onse adzapitako. “Ndithudi palibe munthu amene amalanga munthu wosweka mtima, amene akupempha thandizo mʼmasautso ake. Kodi ine sindinalire nawo iwo amene anali pamavuto? Kodi mtima wanga sunamvere chisoni anthu osauka? Koma pamene ndinkayembekezera zabwino, zoyipa ndiye zinandigwera; pamene ndinkafunafuna kuwala, mdima ndiye unandigwera. Kuwawa kwa mʼkati mwanga sikukuleka; ndili mʼmasiku amasautso. Ndikuyenda wothimbirira, komatu osati ndi dzuwa; ndimayimirira pa msonkhano ndi kupempha chithandizo molira. Ndasanduka mʼbale wa nkhandwe, mnzawo wa akadzidzi. Khungu langa layamba kuda ndipo likufunduka; thupi langa likutentha chifukwa cha kuphwanya kwa thupi. Pangwe wanga wasanduka woyimbira maliro, ndipo chitoliro changa chikuyimbira anthu olira. “Ndinachita pangano ndi maso anga kuti sindidzapenya namwali momusirira. Kodi Mulungu kumwambako wandisungira zotani? Kodi cholowa changa chochokera kwa Wamphamvuzonse kumwambako nʼchotani? Kodi si chiwonongeko kwa anthu oyipa, tsoka kwa iwo amene amachita zolakwa? Kodi Mulungu saona zochita zanga, ndi kudziwa mayendedwe anga? “Ngati ndachita zinthu mwachiphamaso, kapena kufulumira kukachita zachinyengo, Mulungu andiyeze ndi muyeso wake wolungama ndipo Iye adzadziwa kuti ine ndine wosalakwa, ngati mayendedwe anga asempha njira, ngati mtima wanga wakhumbira zimene maso anga aona, kapena ngati ndachita choyipa chilichonse. Pamenepo ena adye zimene ndinadzala, ndipo zomera zanga zizulidwe. “Ngati mtima wanga unakopekapo ndi mkazi, ndipo ngati ndinalakalaka mkazi wa mnansi wanga, pamenepo mkazi wanga aphikire mwamuna wina chakudya, ndipo amuna ena azigona naye. Pakuti zimenezo zikanakhala zochititsa manyazi, tchimo loyenera kulangidwa nalo. Ndi moto umene umayaka mpaka chiwonongeko; ukanapsereza zokolola zanga. “Ngati ndinkapondereza mlandu wa akapolo anga aamuna kapena aakazi, pamene ankabwera kwa ine ndi milandu yawo, ndidzatani pamene Mulungu adzanditsutsa? Nanga ndidzayankha chiyani akadzandifunsa? Kodi amene anapanga ine mʼmimba mwa amayi anga si yemwe anapanganso iwo? Kodi si mmodzi yemweyo amene anatipanga tonsefe mʼmimba mwa amayi athu? “Ngati ndinawamana aumphawi zinthu zimene ankazikhumba, kapena kuwagwiritsa fuwa lamoto akazi amasiye amene amafuna thandizo kwa ine, ngati chakudya changa ndinadya ndekha, wosagawirako mwana wamasiye, chonsechotu kuyambira unyamata wanga ndinamulera monga abambo ake, ndipo moyo wanga wonse ndakhala ndikusamalira akazi amasiye, ngati ndinaona wina aliyense akuzunzika ndi usiwa, kapena munthu wosauka alibe chofunda, ndipo ngati iyeyo sananditamandepo chifukwa chomufunditsa ndi nsalu ya ubweya wankhosa, ngati ndinaopsezapo mwana wamasiye, poganiza kuti ndinali ndi mphamvu mʼbwalo la milandu, pamenepo phewa langa lipokonyeke, mkono wanga ukonyoke polumikizira pake. Popeza ine ndinaopa kwambiri chiwonongeko chochokera kwa Mulungu, ndinachitanso mantha ndi ulemerero wake, sindikanatha kuchita zinthu zimenezi. “Ngati ndinayika mtima wanga pa chuma kapena kunena kwa golide wabwino kwambiri kuti, ‘Iwe ndiye chitetezo changa,’ ngati ndinakondwera chifukwa choti chuma changa chinali chambiri, zinthu zimene manja anga anazipeza, ngati pamene ndinaona dzuwa likuwala, kapena mwezi ukuyenda mwa ulemerero wake, ndipo kuti mtima wanga unakopeka nazo nʼkuyika dzanja langa pakamwa mozilemekeza, pamenepo zimenezinso zikanakhala machimo oti ndilangidwe nawo, chifukwa ndikanakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wakumwamba. “Ngati ndinasangalala ndi kuwonongeka kwa mdani wanga, kapena kusekera mavuto pamene mavuto anamugwera, ine sindinachimwe ndi pakamwa panga potulutsa matemberero a mdani wanga kuti awonongeke, ngati anthu amene ndimakhala nawo mʼnyumba mwanga sananenepo kuti, ‘Kodi ndani amene sakhuta ndi chakudya cha Yobu?’ Komatu mlendo sindinamusiye pa msewu usiku wonse, pakuti khomo langa linali lotsekuka nthawi zonse kwa alendo, ngati ndinabisa tchimo langa monga amachitira anthu ena, kubisa kulakwa mu mtima mwanga chifukwa choopa gulu la anthu, ndi kuchita mantha ndi mnyozo wa mafuko kotero ndinakhala chete ndipo sindinatuluke panja. “Aa, pakanakhala wina wondimva! Tsopano ndikutsiriza mawu anga odzitetezera. Wamphamvuzonse andiyankhe; mdani wanga achite kulemba pa kalata mawu ake ondineneza. Ndithu ine ndikanakoleka kalatayo pa phewa langa, ndikanayivala kumutu ngati chipewa chaufumu. Ndikanamufotokozera zonse zimene ndinachita; ndikanafika pamaso pake ngati kalonga. “Ngati minda yanga ikulira monditsutsa ine ndipo malo ake onse osalimidwa anyowa ndi misozi, ngati ndinadya za mʼminda mwake osapereka ndalama kapena kukhumudwitsa anthu olima mʼmindamo, pamenepo mʼmindamo mumere namsongole mʼmalo mwa tirigu ndi udzu mʼmalo mwa barele.” Mawu a Yobu athera pano. Mawu a Elihu Tsono anthu atatuwa analeka kumuyankha Yobu, chifukwa chakuti iyeyo ankadziona kuti ndi wolungama. Koma Elihu, mwana wa Barakeli, wa fuko la Buzi, wa banja la Ramu, anapsera mtima kwambiri Yobu chifukwa choti Yobuyo anakana kuvomera kuti anachimwa ndi kuti Mulungu anakhoza pomulanga. Anapseranso mtima abwenzi ake atatu aja chifukwa sanapeze njira yomutsutsira Yobu, ngakhale iwo anamupeza kuti anali wolakwa. Tsono Elihu anadikira kuti ayankhule ndi Yobu chifukwa choti abwenziwo anali akuluakulu kupambana iyeyo. Koma Elihu ataona kuti anthu atatuwo analibe mawu oti ayankhulenso, iye anapsa mtima. Choncho Elihu mwana wa Barakeli wa fuko la Buzi anati: “Ine ndine wamngʼono, inuyo ndinu akuluakulu, nʼchifukwa chake ndimaopa, ndimachita mantha kuti ndikuwuzeni zimene ndimadziwa. Ndimaganiza kuti, ‘Ayambe ndi akuluakulu kuyankhula; anthu amvulazakale ndiwo amaphunzitsa nzeru.’ Koma mzimu wa Mulungu mwa munthu, mpweya wa Wamphamvuzonse, ndi umene umapereka nzeru zomvetsa zinthu. Si okalamba amene ali ndi nzeru, si amvulazakale okha amene ali ndi nzeru zomvetsa zinthu zimene zili zoyenera. “Nʼchifukwa chake ndikuti, ‘Mvereni; inenso ndikukuwuzani zimene ndikuzidziwa.’ Ndadikira nthawi yonseyi, ndimamvetsera mwachidwi zimene mumayankhula, pamene mumafunafuna mawu oti muyankhule, ineyo ndinakumvetseranidi. Koma palibe ndi mmodzi yemwe wa inu amene anatsutsa Yobu; palibe aliyense wa inu amene anamuyankha mawu ake. Musanene kuti, ‘Ife tapeza nzeru; Mulungu ndiye amutsutse, osati munthu.’ Koma Yobu sanayankhule motsutsana ndi ine, ndipo ine sindimuyankha monga mmene inu mwamuyankhira. “Iwo asokonezeka ndipo alibe choti ayankhulenso; mawu awathera. Kodi ine ndidikire chifukwa iwo sakuyankhula tsopano, pakuti angoyima phee wopanda yankho? Inenso ndiyankhulapo tsopano; nanenso ndinena zimene ndikudziwa. Pakuti ndili nawo mawu ambiri, ndipo mtima wanga ukundikakamiza; mʼkati mwanga ndili ngati botolo lodzaza ndi vinyo, ngati matumba a vinyo watsopano amene ali pafupi kuphulika. Ndiyenera kuyankhula kuti mtima utsike; ndiyenera kutsekula pakamwa panga ndi kuyankha. Sindidzakondera munthu wina aliyense, kapena kuyankhula zoshashalika, pakuti ndikanakhala wa luso loyankhula moshashalika, Mlengi wanga akanandilanga msanga.” “Koma tsopano, inu abambo Yobu chonde mverani mawu anga; mutcherere khutu zonse zimene ndinene. Tsopano ndiyamba kuyankhula; mawu anga ali pa msonga ya lilime langa. Mawu anga akuchokera mu mtima wolungama; pakamwa panga pakuyankhula zoonadi zimene ndikuzidziwa. Mzimu wa Mulungu wandiwumba, mpweya wa Wamphamvuzonse umandipatsa moyo. Mundiyankhe ngati mungathe; konzekani tsopano kuti munditsutse. Ine ndili monga inu pamaso pa Mulungu; nanenso ndinachokera ku dothi. Musachite mantha ndipo musandiope ayi, Ine sindikupanikizani kwambiri ayi. “Koma inu mwayankhula ine ndikumva, ndamva mawu anuwo onena kuti, ‘Ndine wolungama mtima ndi wopanda tchimo; ndine woyera mtima ndipo ndilibe cholakwa. Komatu Mulungu wapeza zifukwa zoti anditsutsire nazo; Iye akundiyesa ngati mdani wake. Iyeyo wamanga mapazi anga mʼzigologolo, akulonda mayendedwe anga onse.’ “Koma ine ndi kuti kwa inu, inuyo simukukhoza pa zimenezi, pakuti Mulungu ndi wamkulu kupambana munthu. Chifukwa chiyani mukudandaula kwa Iye kuti sayankha mawu ena aliwonse a munthu? Pajatu Mulungu amayankhula mwa njira zosiyanasiyana, ngakhale munthu sazindikira zimenezi. Mʼmaloto, mʼmasomphenya usiku, pamene anthu ali mʼtulo tofa nato pamene akungosinza chabe pa bedi, amawanongʼoneza mʼmakutu ndi kuwaopseza ndi machenjezo ake, kumuchotsa munthu ku zoyipa, ndi kuthetseratu kunyada kwake, kumulanditsa munthu ku manda, kuti moyo wake usawonongeke ndi lupanga. “Mwina Mulungu amalanga munthu ndi matenda ndi ululu ali pa bedi pake, nthawiyo thupi lake lonse limangophwanya, kuti asakhalenso ndi chilakolako cha chakudya, ndipo amanyansidwa ndi chakudya chabwino chomwe. Thupi lake limawonda ndipo mafupa ake, omwe anali obisika, tsopano amaonekera poyera. Munthuyo amayandikira ku manda, moyo wake umayandikira kwa amene amabweretsa imfa. “Koma patakhala mngelo ngati mthandizi, mmodzi mwa ambirimbiri oterewa, adzafotokoza zimene zili zoyenera, kudzamukomera mtima ndi kunena kuti, ‘Mupulumutseni kuti asapite ku manda; ine ndapeza cholowa mʼmalo mwa moyo wake,’ pamenepo thupi lake lidzasanduka lasee ngati la mwana; ndipo adzabwezeretsedwanso kukhala ngati mʼmasiku a unyamata wake. Akapemphera kwa Mulungu, iyeyo adzalandiridwa. Mulungu adzamulandira mwa chimwemwe ndipo adzamubwezeretsa pamalo ake oyamba. Ndipo adzabwera kwa anzake ndi kunena kuti, ‘Ndinachimwa ndipo sindinachite zolungama, koma sindinalangidwe koyenerana ndi kuchimwa kwanga. Iye anapulumutsa moyo wanga kuti usapite ku manda, ndipo ndidzakhala ndi moyo ndi kuonanso kuwala kwa dzuwa.’ “Mulungu amachita zonsezi kwa munthu kawirikawiri, kupulumutsa moyo wa munthuyo ku manda, kuti athe kuonanso kuwala kwa moyo. “Abambo Yobu, tcherani khutu ndipo mundimvere; khalani chete kuti ndiyankhule. Ngati muli nʼchoti munene, ndiyankheni; yankhulani, pakuti ine ndikufuna mupezeke wolungama. Koma ngati sichoncho, mundimvere; khalani chete ndipo ine ndidzakuphunzitsani nzeru.” Pamenepo Elihu anapitiriza kuyankhula kuti, “Imvani mawu anga, inu anthu anzeru; tcherani khutu inu anthu ophunzira. Pakuti khutu limayesa mawu monga momwe mʼkamwa mumalawira chakudya. Tsono tiyeni tizindikire chomwe chili choyenera; tiphunzire pamodzi chomwe chili chabwino. “Yobu akunena kuti, ‘Ndine wosalakwa, koma Mulungu akukana kundiweruza molungama. Ngakhale ndine wolungama mtima, akundiyesa wabodza; ngakhale ndine wosachimwa, mivi yake ikundichititsa mabala osachiritsidwa.’ Kodi munthu wofanana ndi Yobu ndani, amene amayankhula zamwano ngati akumwa madzi? Iye amayenda ndi anthu ochita zoyipa; amayanjana ndi anthu oyipa mtima. Paja iye amanena kuti, ‘Munthu sapindula kanthu poyesetsa kukondweretsa Mulungu.’ “Tsono mverani ine, inu anthu anzeru zomvetsa zinthu. Mulungu sangachite choyipa ndi pangʼono pomwe, Wamphamvuzonse sangathe kuchita cholakwa. Iye amamubwezera munthu molingana ndi ntchito zake; Mulungu amabweretsa pa munthu molingana ndi zomwe amachita. Nʼchosayembekezeka kuti Mulungu achite cholakwa, kuti Wamphamvuzonse apotoze chilungamo. Kodi anapatsa Mulungu udindo wolamulira dziko lapansi ndani? Ndani anayika Mulungu kuti azilamulira dziko lonse? Mulungu akanakhala ndi maganizo oti achotse mzimu wake ndi mpweya wake, zamoyo zonse zikanawonongekeratu ndipo munthu akanabwerera ku fumbi. “Ngati ndinu omvetsa zinthu, imvani izi; mvetserani zimene ndikunena. Kodi Mulungu wodana ndi chilungamo angathe kukhala wolamulira? Kodi iwe ungathe kuweruza Wolungama ndi Wamphamvuyo? Kodi si Iye amene amanena kwa mafumu kuti, ‘Ndinu opanda pake,’ ndipo amawuza anthu otchuka, ‘Ndinu oyipa,’ Iye sakondera akalonga ndipo salemekeza anthu olemera kupambana osauka, pakuti onsewa ndi ntchito ya manja ake? Iwo amafa mwadzidzidzi, pakati pa usiku; anthu amachita mantha ndipo amamwalira; munthu wamphamvu amachotsedwa popanda dzanja la munthu. “Maso a Mulungu amapenya njira za munthu; amaona mayendedwe ake onse. Palibe malo obisika kapena a mdima wandiweyani kumene anthu ochita zoyipa angabisaleko. Mulungu sasowa kuti apitirizebe kufufuza munthu, kuti abwere pamaso pake kudzaweruzidwa. Popanda kufufuza, Iye amawononga anthu amphamvu ndipo mʼmalo mwawo amayikamo ena. Pakuti Iyeyo amadziwa bwino ntchito zawo amawagubuduza usiku ndipo amatswanyika. Iye amawalanga chifukwa cha kuyipa kwawo, pamalo pamene aliyense akuwaona; Chifukwa anasiya kumutsata ndipo sasamaliranso njira zake zonse. Anachititsa amphawi kuti kulira kwawo kufike pamaso pake, kotero Iyeyo anamva kulira kwa amphawiwo. Koma ngati Mulungu akhala chete, ndani angamunene kuti walakwa? Akabisa nkhope yake, ndani angathe kumupenyabe? Komatu ndiye amene amayangʼana za munthu komanso mtundu wa anthu, kuti asalamuliridwe ndi anthu osapembedza, kuti asatchere anthu misampha. “Mwina munthu atanena kwa Mulungu kuti, ‘Ndine wolakwa koma sindidzachimwanso, ndiphunzitseni zimene sindikuziona ngati ndachita choyipa, sindidzachitanso.’ Kodi Mulungu akuweruzeni potsata mmene inuyo mukuganizira, pamene inu mukukana kulapa? Chisankho nʼchanu, osati changa; tsono ndiwuzeni zomwe mukudziwa. “Anthu omvetsa zinthu adzakambirana, anthu anzeru amene akundimva adzandiwuza kuti, ‘Yobu akuyankhula mopanda nzeru; mawu ake ndi opanda fundo.’ Aa, kunali bwino Yobu akanayesedwa mpaka kumapeto chifukwa choyankha ngati munthu woyipa! Pa tchimo lake amawonjezerapo kuwukira; amawomba mʼmanja mwake monyoza pakati pathu, ndipo amachulukitsa mawu otsutsana ndi Mulungu.” Ndipo Elihu anawonjeza kunena kuti, “Kodi mukuganiza kuti mukukhoza? Mukunena kuti, ‘Ndine wolungama pamaso pa Mulungu.’ Komanso inu mukufunsa kuti, ‘Kodi phindu langa nʼchiyani, ndipo ndimapeza chiyani ndikapanda kuchimwa?’ “Ine ndikufuna ndikuyankheni inu pamodzi ndi abwenzi anu omwe. Yangʼanani kumwamba ndipo muone mitambo imene ili kutali ndi inuyo. Inuyo mukachimwa, Iye zimamukhudza motani? Ngati machimo anu ndi ochuluka, zimenezo zimachita chiyani kwa Iye? Ngati inu ndinu wolungama, mumamupatsa Iyeyo chiyani? Kapena Iye amalandira chiyani chochokera mʼdzanja lanu? Kuyipa kwanu kumangokhudza anthu ngati inuyo, ndipo chilungamo chanu chimakhudza anthu anzanu. “Anthu akufuwula chifukwa cha kuzunzidwa; akufuna chithandizo kuti achoke pansi pa ulamuliro wa anthu amphamvu. Koma palibe amene akunena kuti, ‘Kodi ali kuti Mulungu, Mlengi wanga, amene amatisangalatsa nthawi ya usiku, amene amatiphunzitsa kupambana nyama za dziko lapansi ndipo amatipatsa nzeru kupambana mbalame zowuluka?’ Iye sayankha pamene anthu akufuwulira kwa Iye chifukwa cha kudzikuza kwa anthu oyipa. Ndithu, Mulungu samva kupempha kwawo kopanda pake; Wamphamvuzonse sasamalira zimenezi. Ndipo ndi bodza lalikulu kunena kuti Iye saona zimene zikuchitika. Iye adzaweruza molungama ngati inu mutamudikira ndiye tsono popeza kuti ukali wake sukupereka chilango, zoyipa zambiri zimene anthu amachita, abambo Yobu mumangoyankhula zopandapake, mukungochulukitsa mawu opanda nzeru.” Ndipo Elihu anapitirira kuyankhula nati: “Mundilole pangʼono pokha ndipo ndikuonetsani kuti zilipo zambiri zoti ziyankhulidwe mʼmalo mwa Mulungu. Nzeru zanga ndimazitenga kutali; ndidzaonetsa kulungama kwa Mlengi wanga. Ndithudi mawu anga si abodza; wanzeru zangwiro ali ndi inu. “Mulungu ndi wamphamvu, koma sanyoza anthu; Iye ndi wamphamvu, ndipo ndi wokhazikika pa cholinga chake. Salola oyipa kuti akhalebe ndi moyo koma amapereka ufulu kwa anthu osautsidwa. Iye saleka kuyangʼanira anthu olungama; amawayika kuti alamulire pamodzi ndi mafumu ndipo amawalemekeza mpaka muyaya. Koma ngati anthu amangidwa ndi unyolo, ndipo akondwa ndi zingwe zamasautso, Iye amawafotokozera zomwe anachita, kuti iwo anachimwa modzikuza. Mulungu amawatsekula makutu kuti amve malangizo ake ndipo amawalamula kuti alape zoyipa zawo. Ngati iwo amumvera ndi kumutumikira, adzatsiriza masiku a moyo wawo mwamtendere, adzatsiriza zaka zawo mosangalala. Koma ngati samvera, adzaphedwa ndi lupanga ndipo adzafa osadziwa kanthu. “Anthu osapembedza amasunga mkwiyo mu mtima mwawo; akawalanga, safuwulira kwa Iye kupempha thandizo. Amafa akanali achinyamata, pakati pa amuna achiwerewere a kumalo azipembedzo. Koma ovutika, Iye amawapulumutsa pa mavuto awo; Mulungu amawayankhula mʼmasautso awowo. “Iye akukukopani inu kuti muchoke mʼmasautso, kuti mupite ku malo aakulu kumene kulibe chokutchingani, kumalo a mpumulo kumene kuli chakudya chabwino kwambiri. Koma tsopano inu mwapezeka wopalamula chifukwa cha kuyipa kwanu; chiweruzo ndi chilungamo chakugwerani. Muchenjere kuti wina asakukopeni ndi chuma; musalole kuti chiphuphu chachikulu chikusocheretseni. Kodi chuma chanu kapena mphamvu zanu zonse zingakusungeni kotero kuti simungakhale pa masautso? Musalakalake kuti usiku ubwere, pakuti ndiyo nthawi imene anthu adzawonongeka. Muchenjere kuti musatembenukire ku uchimo, chifukwa uchimowo ndiwo unabweretsa kuzunzika kwanu. “Taonani, Mulungu ndi wamkulu ndiponso ndi wamphamvu. Kodi ndi mphunzitsi uti amene angafanane naye? Kodi ndani amene anamuwuzapo Mulungu zoti achite, kapena kumuwuza kuti, ‘Inu mwachita chinthu cholakwa?’ Kumbukirani kutamanda ntchito zake zimene anthu amaziyamika mʼnyimbo. Anthu onse amaziona ntchitozo; anthuwo amaziona ali kutali. Ndithudi, Mulungu ndi wamkulu, sitimudziwa nʼpangʼono pomwe! Chiwerengero cha zaka zake nʼchosadziwika. “Mulungu ndiye amakweza timadontho tamadzi kuthambo, timene timasungunuka nʼkukhala mvula; mitambo imagwetsa mvulayo ndipo mvulayo imavumbwa pa anthu mokwanira. Kodi ndani amene angadziwe momwe mitambo imayendera, momwe Iye amabangulira kuchokera kumalo ake? Taonani momwe amawalitsira zingʼaningʼani pa malo ake onse, zimafika ngakhale pansi pa nyanja. Umu ndi mmene Iye amalamulira mitundu ya anthu ndi kuwapatsa chakudya chochuluka. Amadzaza manja ake ndi zingʼaningʼani, ndipo amazilamulira kuti zigwe pamalo pamene Iye akufuna. Mabingu ake amalengeza za kubwera kwa mvula yamkuntho; ngʼombe nazo zimalengeza za kubwera kwake. “Mtima wanga ukulumphalumpha pa chimenechinso ndipo ukuchoka mʼmalo mwake. Tamverani! Tamverani kubangula kwa liwu lake, kugunda kumene kukuchokera mʼkamwa mwake. Iye amaponya chingʼaningʼani chake pansi pa thambo lonse ndipo amachitumiza ku dziko lapansi. Pambuyo pake kubangula kwake kumamveka. Iye amabangula ndi liwu lake laulemerero. Pamene wabangula, palibe chimene amalephera kuchita. Liwu la Mulungu limabangula mʼnjira zambiri zodabwitsa Iye amachita zinthu zazikulu zimene sitingathe kuzimvetsa. Amalamula chisanu chowundana kuti, ‘Igwa pa dziko lapansi,’ ndipo amalamulanso mvula yamawawa kuti, ‘Khala mvula yamphamvu.’ Kuti anthu onse amene anawalenga athe kuzindikira ntchito yake. Iye amalepheretsa anthu kugwira ntchito zawo. Zirombo zimakabisala ndipo zimakhala mʼmaenje mwawo. Mphepo yamkuntho imatuluka ku malo ake, kuzizira kumatuluka mʼmphepo yamkunthoyo. Mpweya wa Mulungu umawunditsa madzi ndipo madzi a mʼnyanja amawuma kuti gwaa. Iye amadzaza mitambo ndi madzi a mvula, amabalalitsa zingʼaningʼani zake kuchokera mʼmitambomo. Mulungu amayendetsa mitamboyo mozungulirazungulira dziko lonse lapansi kuti ichite zonse zimene Iye akufuna pa dziko lapansi. Iye amagwetsa mvula kuti alange anthu, kapena kubweretsa chinyontho pa dziko lapansi kuti aonetse chikondi chake. “Abambo Yobu, tamvani izi; imani ndipo muganizire ntchito zodabwitsa za Mulungu. Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayendetsera mitambo ndi kuchititsa kuti kukhale zingʼaningʼani? Kodi mukudziwa momwe Mulungu amayalira mitambo, ntchito zodabwitsa za Iye amene ndi wanzeru zangwiro? Inu amene mʼzovala zanu mumatuluka thukuta pamene kunja kwatentha chifukwa cha mphepo yakummwera, kodi mungathe kuthandizana naye kutambasula thambo limene ndi lolimba ngati chitsulo? “Tiwuzeni ife zoti tikanene kwa Iye; sitingathe kufotokoza mlandu wathu chifukwa cha mdima umene uli mwa ife. Kodi nʼkofunika kumudziwitsa Mulungu kuti ndili naye mawu? Kodi kutero sikuchita ngati kupempha kuti ndiwonongeke? Tsopano munthu sangathe kuyangʼana dzuwa, ndi kunyezimira mlengalenga, kuwomba kwa mphepo kutachotsa mitambo yonse. Kuwala kwake kumaonekera cha kumpoto; Mulungu amabwera ndi ulemerero woopsa. Wamphamvuzonse sitingathe kumufikira pafupi ndi wa mphamvu zoposa; pa chiweruzo chake cholungama ndi mʼchilungamo chake chachikulu Iye sapondereza anthu ozunzika. Nʼchifukwa chake anthu amamuopa kwambiri, kodi saganizira za onse amene amaganiza kuti ndi anzeru?” Yehova Ayankhula Apo Yehova anamuyankha Yobu mʼkamvuluvulu. Ndipo anati: “Kodi uyu ndani amene akusokoneza uphungu wanga poyankhula mawu opanda nzeru? Onetsa chamuna; ndikufunsa ndipo undiyankhe. “Kodi unali kuti pamene ndinkayika maziko a dziko lapansi? Ndiwuze ngati ukudziwa. Ndani amene analemba malire ake? Ndithudi iwe ukudziwa! Ndani amene anayeza ndi chingwe dzikoli? Kodi maziko ake anawakumba potani, kapena ndani anayika mwala wake wapangodya, pamene nyenyezi za kummawa zinkayimba pamodzi ndipo angelo onse a Mulungu ankafuwula mokondwa? “Kodi ndani amene anatsekera nyanja pamene inkalengedwa, pamene inkachita ngati kutumphuka pansi pa dziko, pamene ndinasandutsa mitambo kukhala chovala chake ndi kuyikulunga mu mdima wandiweyani, pamene ndinayilembera malire ake ndikuyikira zitseko ndi mipiringidzo yake. Pamene ndinati, ‘Ufike mpaka apa ndipo usapitirire apa ndiye pamene mafunde ako amphamvuwo azilekezera?’ “Kodi chibadwire chako unalamulapo dzuwa kuti lituluke mmawa, kapena kuti mʼbandakucha ukhalepo pa nthawi yake, kuti kuwalako kuwunikire dziko lonse lapansi ndi kuthamangitsa anthu oyipa? Chifukwa cha kuwala kwa usana mapiri ndi zigwa zimaonekera bwino ngati zilembo za chidindo pa mtapo; zimaonekera bwino ngati makwinya a chovala. Kuwala kwa dzuwako sikuwafikira anthu oyipa, ndipo dzanja lawo silingathe kuchita kanthu. “Kodi unayendapo pansi penipeni pa nyanja kapena pa magwero ake ozama? Kodi anakuonetsapo zipata za imfa? Kodi unaonako ku dziko la anthu akufa kumene kuli mdima wandiweyani? Kodi kukula kwa dziko lapansi umakudziwa? Undiwuze ngati ukuzidziwa zonsezi. “Kodi njira yopita kumene kumakhala kuwala ili kuti? Nanga mdima umakhala kuti? Kodi iwe ungathe kuziperekeza kwawoko zimenezi? Kodi ukuyidziwa njira yopita kwawoko? Ndithu, iwe ukuyidziwa, poti paja nthawi imeneyo nʼkuti utabadwa kale! Wakhala ndi moyo zaka zambiridi! “Kodi unalowamo mʼnyumba zosungira chisanu chowundana kapena unayionapo nyumba yosungira matalala, zimene ndazisungira nthawi ya mavuto ndi nthawi yomenyana ndi ya nkhondo? Kodi umadziwa njira ya kumene kumachokera chingʼaningʼani kapena njira ya kumene kumachokera mphepo ya kummawa imene ili pa dziko lonse lapansi? Kodi ndani amene amakonza ngalande za mvula, nanga ndani anakonza njira yoyendamo mphenzi, kuthirira madzi dziko limene sikukhala munthu, chipululu chopandamo munthu, kukhutitsa nthaka yowuma yagwaa ndi kumeretsamo udzu? Kodi mvula ili ndi abambo ake? Nanga madzi a mame anawabereka ndani? Kodi madzi owundana anawabereka ndani? Ndani amene anabereka chisanu chochokera kumwamba pamene madzi amawuma gwaa ngati mwala, pamene madzi a pa nyanja amazizira, nalimba kuti gwaa? “Kodi iwe ungayimitse kuyenda kwa nyenyezi? Kodi ungathe kuletsa kuyenda kwa nsangwe ndi akamwiniatsatana? Kodi ungathe kuwongolera nyenyezi pa nyengo yake kapena kutsogolera nyenyezi yayikulu ya chimbalangondo pamodzi ndi ana ake? Kodi malamulo a mlengalenga umawadziwa? Kodi ungathe kukhazikitsa ulamuliro wa Mulungu pa dziko lapansi? “Kodi iwe ungathe kulamula mitambo kuti igwetse mvula ya chigumula? Kodi ungathe kutumiza zingʼaningʼani kuti zingʼanime? Kodi zimabwera pamaso pako ndi kuti, ‘Tili pano?’ Kodi ndani anayika nzeru mu mtima, ndani analonga mʼmaganizo nzeru zomvetsa zinthu? Wanzeru ndani amene angathe kuwerenga mitambo? Ndani angathe kupendeketsa mitsuko ya madzi akuthambo pamene fumbi limasanduka matope, ndipo matopewo amawumbika? “Kodi ndani amawusakira chakudya mkango waukazi ndi kukhutitsa misona ya mikango pamene ili khale mʼmapanga mwawo kapena pamene ikubisala pa tchire? Kodi amamupatsa khwangwala chakudya chake ndani pamene ana ake akulirira kwa Mulungu ndi kumayendayenda chifukwa chosowa zakudya? “Kodi iwe umadziwa nthawi imene mbalale yayikazi imaswera? Kodi umaonerera pamene nswala ikubala? Kodi umawerenga miyezi imene zimakhala ndi bere? Kodi nthawi imene zimaswana iwe umayidziwa? Zimakhala tsonga ndi kuswa ana awo; pamenepo ululu wobereka nʼkutha. Ana a nyamazi amakhala ndi mphamvu ndipo amakulira mʼthengo; kenaka amachoka ndipo sabwereranso. “Kodi bulu wakuthengo amamupatsa ndani ufulu wongodziyendera? Ndani amamasula zingwe zake? Ine ndinamupatsa chipululu kuti chikhale mudzi wake, nthaka ya mchere kuti ikhale malo ake okhalamo Iye amakhala kutali ndi phokoso la mu mzinda; ndipo samva kufuwula kwa oyendetsa nyama zakatundu. Amayendayenda mʼmapiri kudya msipu ndipo amafunafuna msipu uliwonse wobiriwira. “Kodi njati ingavomere kukutumikira? Kodi ingagone mu gome lako usiku? Kodi ungathe kuyimanga ndi zingwe kuti izilima? Kodi ingasalaze nthumbira mʼmunda mwako? Kodi ungadalire njatiyo chifukwa champhamvu zake? Kodi ungayilekere kuti igwire ntchito zako zolemetsa? Kodi ungadalire kuti idzakubweretsera tirigu wako ndi kumuyika ku malo opunthira? “Nthiwatiwa imakupiza mapiko ake monyadira, koma mapikowo sangafanane ndi mapiko ndi nthenga za kakowa. Nthiwatiwa imakwirira mazira ake pansi ndipo amafundidwa ndi nthaka, nthiwatiwayo sidera nkhawa kuti mazira ake angathe kuswanyidwa, ndi kuti nyama zakuthengo zitha kuwaponda. Nthiwatiwa imachitira nkhanza ana ake ngati anawo si ake; Imayiwala zoti inavutika powabala. Chifukwa Mulungu anayimana nzeru, simvetsa kanthu kalikonse. Komatu nthiwatiwa ikadzambatuka ndi kuyamba kuthamanga, imamusiya kutali kavalo ndi wokwerapo wake. “Kodi ndiwe amene umamupatsa mphamvu kavalo kapena kumuveka chenjerere mʼkhosi mwake? Kodi ndiwe amene umalipatsa dzombe ulemerero wolumphira, ukali wake nʼkumachititsa mantha? Iye amalumphalumpha moopseza, kukondwerera mphamvu zake, ndipo amapita ku nkhondo ndi mphamvu zake zonse. Iye sachita mantha, saopa chilichonse; sabwerera mʼmbuyo akaona lupanga. Zida zankhondo zimachita kwichikwichi mʼchimake pambali pake pamodzi ndi mkondo wonyezimira ndi nthungo. Kavaloyo amanjenjemera ndi ukali ndi kulumphalumpha; satha kungoyima pamene wamva kulira kwa lipenga. Lipenga likalira amati, ‘Twee!’ Amamva fungo la nkhondo ali patali, kufuwula kwa anthu olamulira nkhondo ndi mfuwu wankhondo. “Kodi kabawi amawuluka ndi nzeru zako, ndi kutambasula mapiko ake kupita kummwera? Kodi umalamulira chiwombankhanga ndiwe kuti chiziwuluka ndi kumanga chisa chake pamwamba penipeni? Chimakhala pa phiri ndipo chimakhala pamenepo usiku; chimakhala pa msonga penipeni pa mwala. Chili pamenepo chimayangʼanayangʼana choti chigwire kuti chidye; maso ake amachionera patali chinthucho. Ana ake amayamwa magazi, ndipo kumene kuli mitembo ndiko chimapezeka.” Yehova anati kwa Yobu: “Kodi iwe ufuna kukangana ndi Wamphamvuzonse? Iwe amene unatsutsana ndi Mulungu umuyankhe Iyeyo!” Pamenepo Yobu anayankha Yehova: “Ine sindili kanthu konse, kodi ndingathe kukuyankhani chiyani? Ndagwira pakamwa panga. Ndinayankhula kamodzi, koma pano ndilibe yankho, ndinayankha kawiri, koma sindiwonjezeranso mawu ena.” Ndipo Yehova anayankha Yobu mʼkamvuluvulu kuti, “Tsopano vala dzilimbe ngati mwamuna; ndikufunsa mafunso ndipo iwe undiyankhe. “Kodi iwe unganyoze chiweruzo changa cholungama? Kodi ungandidzudzule kuti iweyo ukhale wolungama? Kodi uli ndi dzanja monga la Mulungu, ndipo mawu ako angagunde ngati mphenzi monga a Mulungu? Ngati zili choncho udzikometsere ndi ulemerero ndi kukongola, ndipo udziveke ulemu ndi ulemerero waufumu. Tsanula ukali wako wosefukirawo, uyangʼane aliyense wodzikuza ndipo umuchepetse, Uyangʼane aliyense wodzikweza ndipo umutsitse, uwapondereze oyipa onse pamalo pomwe alilipo. Onsewo uwakwirire pamodzi mfumbi; ukulunge nkhope zawo mʼmanda. Ukatero Ine ndidzakuvomereza kuti dzanja lako lamanja lakupulumutsadi. “Taganiza za mvuwu, imene ndinayipanga monga momwe ndinapangira iwe, ndipo imadya udzu ngati ngʼombe. Mphamvu zake ndi zazikulu kwambiri, thupi lake ndi lanyonga kwambiri! Mchira wake umayima tolotolo ngati mtengo wamkungudza; mitsempha ya ntchafu zake ndi yogwirana bwino. Mafupa ake ali ngati mapayipi amkuwa, nthiti zake zili ngati mipiringidzo yachitsulo. Mvuwuyo ndi yayikulu mwa zolengedwa za Mulungu, komatu mlengi wake amatha kuyiopseza ndi lupanga lake. Imapeza chakudya chake ku mtunda ndipo nyama zakuthengo zonse zimasewera pambali pake. Imagona pa tsinde pa zitsamba za mipeta, imabisala mʼbango ndiponso pa thawale. Imaphimbika ndi mthunzi wazitsamba za mipeta; imazunguliridwa ndi misondozi ya mu mtsinje. Madzi a mu mtsinje akakokoma, sichita mantha, iyo sitekeseka, ngakhale madzi a mu Yorodani afike mʼkhosi mwake. Kodi alipo amene angathe kukola mvuwu ndi mbedza kapena kuyikola mu msampha? “Kodi ungathe kukoka ngʼona ndi mbedza ya nsomba kapena kukanikiza lilime lake pansi ndi chingwe? Kodi ungathe kumanga chingwe mʼmphuno mwake, kapena kubowola nsagwada zake ndi mbedza? Kodi ngʼonayo idzakupempha kuti uyichitire chifundo? Kodi idzakuyankhula ndi mawu ofatsa? Kodi idzachita nawe mgwirizano kuti uyisandutse kapolo wako mpaka muyaya? Kodi udzasewera nayo ngati mbalame, kapena kuyimangirira kuti atsikana ako asewere nayo? Kodi anthu adzayitsatsa malonda? Nanga amalondawo nʼkugawanagawana nyama yake kuti akagulitse? Kodi chikopa chake ungathe kuchilasa ndi zisonga, kapena kubowola mutu wake ndi nthungo zophera nsomba? Ukayiputa udziwe kuti pali nkhondo, ndipo iweyo sudzabwereranso. Chiyembekezo choti nʼkuyigonjetsa ndi chabodza; kungoyiona kokha, ndithu iwe kumangodzigwera wekha. Palibe wolimba mtima kuti ndi kuyiputa. Ndani angalimbe mtima kulimbana ndi Ine? Kodi ndani anandipatsa kanthu kuti ndimubwezere? Zonse za pansi pa thambo ndi zanga. “Sindidzaleka kuyankhula za ziwalo zake za chirombocho, za mphamvu zake ndiponso za maonekedwe a thupi lake. Ndani angasende chikopa chake? Ndani angayiyandikire kuti abowole chikopa chake cholimbacho? Ndani angatsekule kukamwa kwake, pakamwa pamene pazunguliridwa ndi mano ochititsa mantha? Kumsana kwake kuli mizere ya mamba onga zishango zolumikizanalumikizana; Mambawo ndi olukanalukana kotero kuti mpweya sungathe kulowa pakati pake. Ndi olumikizanalumikizana; ndi omatirirana kwambiri kotero kuti sangathe kulekana. Kuyetsemula kwake kumatulutsa mbaliwali; maso ake amawala ngati kuwala kwa mʼbandakucha. Mʼkamwa mwake mumatuluka nsakali zamoto ndipo mumathetheka mbaliwali zamoto. Mʼmphuno mwake mumatuluka utsi ngati wa mʼnkhali yowira yomwe ili pa moto wa bango. Mpweya wake umayatsa makala, ndipo malawi amoto amatuluka mʼkamwa mwake. Mphamvu zake zili mʼkhosi mwake; aliyense wokumana nayo amangoti njenjenje ndi mantha. Minyewa ya thupi lake ndi yolumikizana ndipo ndi yokhwima kwambiri ndi yolimba. Pachifuwa pake ndi powuma ngati mwala, ndi pa gwaa, ngati mwala wamphero. Ngʼonayo ikangovuwuka, ndi anthu amphamvu omwe amaopa; amabwerera mʼmbuyo, kuthawa. Ngakhale ikanthidwe ndi lupanga, lupangalo silichita kanthu, ngakhale mkondo, muvi ndi nthungo, zonse zimalephera. Chitsulo imachiyesa ngati phesi chabe ndi mkuwa ngati chikuni chowola. Muvi sungathe kuyithawitsa, miyala imene ayilasa nayo imangoyinyenyanyenya. Zibonga zimakhala ngati ziputu; imangoseka pamene akuyibaya ndi nthungo. Mamba a ku mimba kwake ali ngati chopunthira chakunthwa ndipo imasiya mkukuluzi mʼmatope ngati galeta lopunthira tirigu. Imagadutsa madzi ozama ngati madzi a mʼnkhali, imachititsa nyanja kuti iwire ngati mbiya yoyengera mafuta. Kumbuyo kwake imasiya nthubwitubwi zambee, kotero kuti munthu angaganize kuti nyanja yachita imvi. Pa dziko lapansi palibe china chofanana nacho, nʼcholengedwa chopanda mantha. Chimanyoza nyama zina zonse; icho chija ndi mfumu ya nyama zonse.” Yobu Pamenepo Yobu anayankha Yehova kuti, “Ndikudziwa kuti Inu mungathe kuchita zinthu zonse; chimene mufuna kuchita wina sangaletse konse. Munandifunsa kuti, ‘Kodi ndiwe yani amene ukufuna kusokoneza uphungu wanga ndi mawu opanda nzeru? Zoonadi ndinayankhula zimene sindinazimvetse, zinthu zodabwitsa kwambiri kwa ine zimene sindinazidziwe. “Inu munandiwuza kuti, ‘Mvetsetsa tsopano ndipo ndidzayankhula; ndidzakufunsa ndipo iwe udzandiyankhe.’ Ndinkangomva za Inu ndi makutu anga, koma tsopanonso ndakuonani ndi maso anga. Nʼchifukwa chake ndi kuchita manyazi, ndikulapa podzithira fumbi ndi phulusa.” Mulungu Adalitsa Yobu Yehova atayankhula ndi Yobu mawu amenewa anawuza Elifazi wa ku Temani kuti, “Ine ndakukwiyira pamodzi ndi abwenzi ako awiri, chifukwa simunayankhule zabwino za Ine, monga mmene wayankhulira mtumiki wanga Yobu. Kotero tsopano mutenge ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri ndi kupita nazo kwa mtumiki wanga Yobu kuti mukapereke nsembe zopsereza. Mtumiki wanga Yobu adzakupemphererani, ndipo Ine ndidzalandira pemphero lake. Sindidzakuchitirani kanthu molingana ndi uchitsiru wanu. Inu simunayankhule zabwino za Ine, monga anayankhulira Yobu mtumiki wanga.” Motero Elifazi wa ku Temani, Bilidadi wa ku Suki ndi Zofari wa ku Naama anachita zimene Yehova anawawuza ndipo Yehova anamvera pemphero la Yobu. Yobu atawapempherera abwenzi ake aja, Yehova anamubwezera chuma chake ndipo anamupatsa mowirikiza kuposa zomwe anali nazo kale. Abale ake ndi alongo ake onse, kuphatikizapo onse amene ankamudziwa kale, amabwera kwa iye nʼkudzadya naye chakudya mʼnyumba mwake. Iwo anamutonthoza ndi kumupepesa chifukwa cha mavuto onse amene Yehova analola kuti amugwere. Aliyense wa iwowa anamupatsa ndalama ndi mphete yagolide. Yehova anadalitsa Yobu pa masiku ake otsirizawa kupambana poyamba paja. Iye anali ndi nkhosa 14,000, ngamira 6,000, ngʼombe zantchito 2,000 ndi abulu aakazi 1,000. Anaberekanso ana aamuna asanu ndi awiri ndi ana aakazi atatu. Mwana wake wamkazi woyamba anamutcha Yemima, wachiwiri anamutcha Keziya, wachitatu anamutcha Kereni Hapuki. Mʼdziko monsemo munalibe akazi okongola ngati ana a Yobu, ndipo abambo awo anawapatsa cholowa pamodzi ndi alongo awo. Zitachitika zimenezi, Yobu anakhala ndi moyo zaka 140. Iye anaona zidzukulu zake mpaka mʼbado wachinayi. Potsiriza, Yobu anamwalira ali nkhalamba ya zaka zochuluka kwambiri.