- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
YOHANE
Uthenga Wabwino wa Yesu Khristu Wolembedwa ndi Yohane
Yohane
Yoh
UTHENGA WABWINO WA YESU KHRISTU WOLEMBEDWA NDI
YOHANE
Mawu Asandulika Thupi
Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu ndiye Mulungu. Mawuwa anali ndi Mulungu pachiyambi.
Zinthu zonse zinalengedwa ndi Iye; ndipo popanda Iye sikukanakhala kanthu kalikonse kolengedwa. Mwa Iye munali moyo, ndipo moyowo unali kuwunika kwa anthu. Kuwunika kunawala mu mdima, koma mdimawo sunakuzindikire.
Kunabwera munthu amene anatumizidwa kuchokera kwa Mulungu; Iyeyo dzina lake linali Yohane. Iye anabwera ngati mboni kudzachitira umboni kuwunikako kuti kudzera mwa iye anthu onse akhulupirire. Iyeyu sanali kuwunika; koma anabwera ngati mboni ya kuwunika. Kuwunika koona kumene kuwunikira munthu aliyense kunabwera ku dziko lapansi.
Iye anali mʼdziko lapansi, ndipo ngakhale kuti dziko lapansi linalengedwa ndi Iye, dziko lapansilo silinamuzindikire Iye. Iye anabwera kwa iwo amene anali akeake, koma akewo sanamulandire Iye. Koma kwa onse amene anamulandira Iye, kwa amene anakhulupirira mʼdzina lake, Iye anawapatsa mphamvu yokhala ana a Mulungu; ana wobadwa osati monga mwachilengedwe, kapena chisankho cha munthu, kapena chifuniro cha mwamuna koma wobadwa mwa Mulungu.
Mawu anasandulika thupi ndipo anakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wa Iye amene ndi Mwana mmodzi yekhayo wa Atate, wodzaza ndi chisomo ndi choonadi.
Yohane achitira umboni za Iye. Iye akufuwula kuti, “Uyu ndi Iye amene ndinati, ‘Iye amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa, Iyeyo analipo ine ndisanabadwe.’ ” Kuchokera mʼkuchuluka kwa chisomo chake ife tonse talandira madalitso pamwamba pa madalitso. Pakuti lamulo linapatsidwa kudzera mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinabwera kudzera mwa Yesu Khristu. Palibe munthu amene anaona Mulungu, koma Mwana mmodzi yekhayo amene ali wa pamtima pa Atate, ndiye anafotokoza za Iye.
Yohane Mʼbatizi Akana kuti Iye ndi Khristu
Tsopano uwu ndi umboni wa Yohane pamene Ayuda a ku Yerusalemu anatumiza ansembe ndi Alevi kudzamufunsa kuti iye anali yani. Iye sanalephere kuvomereza, koma iye anavomereza momasuka kuti, “Ine sindine Khristu.”
Iwo anamufunsa kuti, “Nanga iwe ndiwe yani? Kodi ndiwe Eliya?”
Iye anati, “Sindine.”
“Kodi ndiwe Mneneri?”
Iye anayankha kuti, “Ayi.”
Pomaliza iwo anati, “Ndiwe yani? Tipatse yankho kuti tipite nalo kwa amene anatituma. Kodi iwe ukuti chiyani za iwe mwini?”
Yohane anayankha ndi mawu a mneneri Yesaya kuti, “Ine ndi mawu a wofuwula mʼchipululu, ‘Wongolani njira ya Ambuye.’ ”
Tsopano Afarisi ena amene anatumidwa anamufunsa Iye kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani, umabatiza ngati iwe si Khristu, kapena Eliya, kapena Mneneri?”
Yohane anayankha kuti, “Ine ndimabatiza ndi madzi, koma pakati panu payima amene simukumudziwa. Iye ndi amene akubwera pambuyo panga, ine siwoyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”
Zonsezi zinachitika ku Betaniya kutsidya lina la mtsinje wa Yorodani, kumene Yohane ankabatizira.
Yesu Mwana Wankhosa wa Mulungu
Pa tsiku lotsatira Yohane anaona Yesu akubwera kwa iye ndipo anati, “Taonani, Mwana Wankhosa wa Mulungu, amene achotsa tchimo la dziko lapansi! Uyu ndi amene ndimatanthauza pamene ndinanena kuti, ‘Munthu amene akubwera pambuyo panga ndi wondiposa ine chifukwa analipo ine ndisanabadwe.’ Ine mwini sindinamudziwe Iye, koma ndinabwera kubatiza ndi madzi kuti Iye adziwike mu Israeli.”
Kenaka Yohane anapereka umboni uwu: “Ine ndinaona Mzimu Woyera ngati nkhunda kuchokera kumwamba nakhala pa Iye. Ine sindikanamudziwa Iye, koma kuti amene anandituma ine kudzabatiza ndi madzi anati kwa ine, ‘Munthu amene udzaona Mzimu Woyera akutsika nakhazikika pa Iye ndi amene adzabatize ndi Mzimu Woyera.’ Ine ndaona ndipo ndikuchitira umboni kuti uyu ndi Mwana wa Mulungu.”
Ophunzira Oyamba a Yesu
Pa tsiku lotsatira Yohane analinso pamenepo pamodzi ndi awiri a ophunzira ake. Iye ataona Yesu akudutsa anati, “Taonani Mwana Wankhosa wa Mulungu!”
Ophunzira ake awiriwo atamva iye akunena izi, iwo anamutsatira Yesu. Atatembenuka, Yesu anaona iwo akumutsatira ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?”
Iwo anati, “Rabi (kutanthauza kuti Aphunzitsi), kodi mukukhala kuti?”
Iye anayankha kuti, “Bwerani mudzaone.”
Choncho iwo anapita ndi kukaona kumene Iye amakhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Linali ngati pafupifupi ora la khumi.
Andreya mʼbale wake wa Simoni Petro, anali mmodzi wa awiriwo amene anamva zimene Yohane ananena ndiponso amene anamutsata Yesu. Choncho chimene Andreya anachita ndi kukapeza mʼbale wake Simoni ndipo anamuwuza kuti, “Ife tamupeza Mesiya,” (kutanthauza kuti Khristu).
Kenaka iye anabweretsa Simoni kwa Yesu, amene anamuyangʼana ndipo anati, “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Udzatchedwa Kefa” (limene litanthauza kuti Petro).
Yesu Ayitana Filipo ndi Natanieli
Pa tsiku lotsatira Yesu anaganiza zopita ku Galileya. Atamupeza Filipo, anati kwa iye, “Nditsate.”
Filipo monga Andreya ndi Petro, anali wochokera ku mzinda mudzi Betisaida. Filipo anakapeza Natanieli ndipo anamuwuza kuti, “Ife tapeza amene Mose analemba za Iye mʼmalamulo, ndi zimene aneneri analembanso za Iye, Yesu wa ku Nazareti, mwana wa Yosefe.”
Natanieli anafunsa kuti, “Nazareti! Kodi kanthu kalikonse kabwino kangachokere kumeneko?”
Filipo anati, “Bwera udzaone.”
Yesu atamuona Natanieli akuyandikira, anati kwa iye, “Uyu ndi Mwisraeli weniweni, mwa iye mulibe chinyengo.”
Natanieli anafunsa kuti, “Kodi mwandidziwa bwanji?”
Yesu anayankha kuti, “Ine ndinakuona iwe utakhala pansi pamtengo wamkuyu Filipo asanakuyitane.”
Kenaka Natanieli ananena kuti, “Rabi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu; Inu ndinu Mfumu ya Israeli.”
Yesu anati, “Ukukhulupirira chifukwa chakuti ndakuwuza kuti Ine ndinakuona iwe uli pansi pamtengo wamkuyu? Iwe udzaona zinthu zazikulu kuposa izo.” Ndipo Iye anapitirira kuti, “Zoonadi, Ine ndikuwuza kuti iwe udzaona kumwamba, kutatsekuka ndi angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika pa Mwana wa Munthu.”
Yesu Asandutsa Madzi Kukhala Vinyo
Pa tsiku lachitatu munali ukwati mu Kana wa ku Galileya. Amayi ake a Yesu anali komweko, ndipo Yesu ndi ophunzira ake anayitanidwanso ku ukwatiwo. Vinyo atatha, amayi a Yesu anati kwa Iye, “Wawathera vinyo.”
Yesu anayankha kuti, “Amayi, chifukwa chiyani mukundiwuza Ine? Nthawi yanga sinakwane.”
Amayi ake anati kwa antchito, “Inu muchite chilichonse chimene akuwuzeni.”
Pamenepo panali mitsuko yamiyala yothiramo madzi isanu ndi umodzi, imene Ayuda amagwiritsa ntchito pa mwambo wodziyeretsa. Uliwonse unali ndi malita 100 kapena kupitirirapo.
Yesu anati kwa antchitowo, “Dzazani madzi mʼmitsukoyi,” ndipo iwo anadzaza ndendende.
Ndipo Iye anatinso kwa iwo, “Tsopano tungani ndipo kaperekeni kwa mkulu waphwando.”
Iwo anachita momwemo. Mkulu waphwando analawa madziwo amene anasandulika vinyo, ndipo sanazindikire kumene vinyoyo anachokera, ngakhale kuti antchito amene anatunga madziwo amadziwa. Kenaka anayitanira mkwati pambali ndipo anati, “Aliyense amatulutsa vinyo wokoma kwambiri poyambirira ndipo kenaka vinyo wosakoma pamene oyitanidwa atamwa kale wambiri; koma iwe wasunga wokoma mpaka tsopano.”
Ichi chinali chizindikiro chodabwitsa choyamba chimene Yesu anachita ku Kana wa ku Galileya. Potero Iye anawulula ulemerero wake, ndipo ophunzira ake anamukhulupirira Iye.
Yesu Ayeretsa Nyumba ya Mulungu
Zitatha izi Iye anatsikira ku Kaperenawo pamodzi ndi amayi ake, abale ake ndi ophunzira ake. Iwo anakhala kumeneko masiku owerengeka.
Nthawi ya Paska ya Ayuda itayandikira, Yesu anapita ku Yerusalemu. Mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu Iye anapeza anthu akugulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda ndipo ena akusintha ndalama pa matebulo. Chifukwa cha zimenezi Iye anapanga chikwapu cha zingwe ndipo anatulutsa onse mʼbwalo la Nyumbayo, pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe; Iye anamwaza ndalama zawo ndi kugudubuza matebulo. Kwa amene amagulitsa nkhunda, Iye anati, “Tulutsani izi muno! Osasandutsa Nyumba ya Atate anga msika!”
Ophunzira ake anakumbukira kuti zinalembedwa kuti, “Kudzipereka kwanga ku nyumba yanu kudzandiphetsa.”
Kenaka Ayuda anamufunsa Yesu kuti, “Kodi mungationetse chizindikiro chodabwitsa chotani chotsimikizira ulamuliro wanu wochitira izi?”
Yesu anawayankha kuti, “Gwetsani Nyumba ya Mulunguyi ndipo Ine ndidzayimanganso mʼmasiku atatu.”
Ayuda anayankha kuti, “Zinatenga zaka makumi anayi kumanga Nyumbayi, kodi Inu mungayimange masiku atatu?” Koma Nyumba ya Mulungu imene amanena linali thupi lake. Iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira zimene Iye ananena ndipo anakhulupirira Malemba ndi mawu amene Yesu anayankhula.
Tsopano Iye ali mu Yerusalemu pa phwando la Paska, anthu ambiri anaona zizindikiro zodabwitsa zimene amachita ndipo anakhulupirira dzina lake. Koma Yesu sanawakhulupirire iwo, pakuti amadziwa anthu onse. Iye sanafune umboni wa wina aliyense popeza amadziwa zomwe zinali mʼmitima mwa anthu.
Yesu Aphunzitsa Nekodimo za Kubadwa Kwatsopano
Ndipo panali Mfarisi wotchedwa Nekodimo, wa mʼgulu lolamulira la Ayuda. Iye anabwera kwa Yesu usiku ndipo anati, “Rabi, ife tikudziwa kuti ndinu aphunzitsi wochokera kwa Mulungu, pakuti palibe amene angachite zizindikiro zodabwitsa zimene Inu mukuchita ngati Mulungu sali naye.”
Poyankha Yesu ananena kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti, ngati munthu sabadwanso mwatsopano sangathe kuona ufumu wa Mulungu.”
Nekodimo anati, “Kodi munthu angabadwenso bwanji atakalamba? Kodi angalowe kachiwiri mʼmimba ya amayi ake kuti abadwenso?”
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu Woyera, sangalowe mu ufumu wa Mulungu. Thupi limabereka thupi, koma Mzimu amabereka mzimu. Iwe usadabwe chifukwa ndakuwuza kuti, ‘Uyenera kubadwanso.’ Mphepo imawomba kulikonse kumene ikufuna. Ungathe kumva kuwomba kwake, koma sungathe kudziwa kumene ikuchokera kapena kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi amene abadwa ndi Mzimu Woyera.”
Nekodimo anafunsa kuti, “Kodi izi zingatheke bwanji?”
Yesu anati, “Iwe mphunzitsi wa Israeli, kodi sukuzindikira zimenezi? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti ife tiyankhula zimene tikuzidziwa ndi kuchitira umboni zimene taziona, komabe inu simuvomereza umboni wathu. Ine ndikuyankhula kwa iwe zinthu za dziko lapansi ndipo sukukhulupirira. Nanga kodi udzakhulupirira bwanji ngati nditayankhula zinthu zakumwamba? Palibe wina aliyense anapita kumwamba, koma yekhayo amene watsika kuchokera kumwamba, Mwana wa Munthu. Tsono monga Mose anapachika njoka mʼchipululu, moteronso Mwana wa Munthu ayenera kupachikidwa, kuti aliyense amene akhulupirira Iye akhale ndi moyo wosatha.
“Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”
Yohane Mʼbatizi Achita Umboni za Yesu
Zitatha izi, Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼmadera a ku midzi ya ku Yudeya, kumene Iye anakhala kanthawi akubatiza. Ndipo Yohane amabatizanso ku Ainoni kufupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri ndipo anthu amabwererabwererabe kudzabatizidwa. (Apa nʼkuti Yohane asanatsekeredwe mʼndende). Mkangano unabuka pakati pa ophunzira ena a Yohane ndi Ayuda ena pa zamwambo wodziyeretsa wa Ayuda. Iwo anabwera kwa Yohane anati, “Rabi, munthu uja munali naye mbali inayo ya mu mtsinje wa Yorodani, amene munamuchitira umboni, taonani naye akubatizanso, ndipo aliyense akupita kwa Iye.”
Atamva zimenezi, Yohane anayankha kuti, “Munthu amalandira chokhacho chapatsidwa kwa iye kuchokera kumwamba. Inuyo ndinu mboni zanga kuti ine ndinati, ‘Ine sindine Khristu koma ndatumidwa patsogolo pa Iye.’ Mwini wake wa mkwatibwi ndi mkwati. Ndipo bwenzi lamkwati limadikira ndi kumvetsera iye, ndipo amakondwa akamva mawu a mkwatiyo. Ine changa ndi chimwemwe ndipo ndine wosangalala kwambiri. Nʼkoyenera kuti Iyeyo akule, ine ndichepe.
“Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”
Yesu Acheza ndi Mayi wa ku Samariya
Yesu atazindikira kuti Afarisi amva zoti Iye ankapeza ndi kubatiza ophunzira ambiri kupambana Yohane, (ngakhale kuti Yesuyo sankabatiza, koma ophunzira ake). Iye anachoka ku Yudeya ndi kubwereranso ku Galileya.
Ndipo Iye anayenera kudutsa mu Samariya. Iye anafika mʼmudzi wa Asamariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi malo amene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe. Chitsime cha Yakobo chinali pamenepo ndipo Yesu atatopa ndi ulendo anakhala pansi pambali pa chitsimecho. Nthawi inali pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi masana.
Mayi wa Chisamariya atabwera kudzatunga madzi, Yesu anati kwa iye, “Kodi ungandipatse madzi akumwa.” (Ophunzira ake nʼkuti atapita mʼmudzi kukagula chakudya).
Mayiyo anati kwa Iye, “Inu ndinu Myuda ndipo ine ndine Msamariya. Bwanji mukundipempha madzi akumwa?” (Popeza Ayuda ndi Asamariya sankayanjana).
Yesu anamuyankha kuti, “Koma iwe ukanadziwa mphatso ya Mulungu ndi Iye amene akukupempha madzi akumwa, ukanamupempha ndipo akanakupatsa madzi amoyo.”
Mayiyo anati, “Ambuye, Inu mulibe kanthu kotungira madzi ndipo chitsime ndi chakuya. Kodi madzi amoyowo mungawatenge kuti? Kodi Inu ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi ndipo iye ankamwanso monga anachita ana ake ndi ziweto zake?”
Yesu anayankha kuti, “Aliyense amene amamwa madzi awa amamvanso ludzu, koma aliyense amene adzamwa madzi amene Ine ndidzamupatsa sadzamvanso ludzu. Ndithudi, madzi amene ndidzamupatsa adzakhala kasupe wamadzi wotumphukira ku moyo wosatha.”
Mayiyo anati kwa Iye, “Ambuye, patseni madzi amenewo kuti ndisadzamvenso ludzu ndi kumabwerabe kuno kudzatunga madzi.”
Iye anamuwuza kuti, “Pita kayitane mwamuna wako ndipo ubwere naye.”
Iye anayankha kuti, “Ine ndilibe mwamuna.”
Yesu anati kwa iye, “Wakhoza ponena kuti ulibe mwamuna. Zoona nʼzakuti iwe wakhala pa banja ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene uli naye tsopano si wako. Zimene wanenazi ndi zoona.”
Mayiyo anati, “Ambuye, ine ndazindikira kuti Inu ndinu mneneri. Makolo athu ankapembedza mʼphiri ili koma inu Ayuda mumati malo amene tiyenera kupembedzera ali ku Yerusalemu.”
Yesu anati, “Mayi inu khulupirira Ine. Nthawi ikubwera pamene inu simudzapembedza Atate mʼphiri ili kapena mu Yerusalemu. Inu Asamariya mumapembedza chimene simukuchidziwa. Ife timapembedza chimene tikuchidziwa, pakuti chipulumutso nʼchochokera kwa Ayuda. Koma nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano pamene opembedza woona adzapembedza Atate mu mzimu ndi mʼchoonadi, pakuti opembedza otere ndiwo amene Atate akuwafuna. Mulungu ndi Mzimu, ndipo omupembedza Iye ayenera kumupembedza mu mzimu ndi mʼchoonadi.”
Mayiyo anati, “Ine ndikudziwa kuti Mesiya (wotchedwa Khristu) akubwera. Akabwera, Iye adzafotokoza zonse kwa ife.”
Ndipo Yesu anamuwuza kuti, “Amene ndikukuyankhulane, ndine amene.”
Ophunzira Abweranso kwa Yesu
Pa nthawi yomweyo ophunzira ake anabwerera ndipo anadabwa kupeza Iye akuyankhula ndi mayi. Koma palibe amene anamufunsa kuti, “Kodi mukufuna chiyani?” kapena, “Nʼchifukwa chiyani mukuyankhula naye?”
Kenaka mayiyo anasiya mtsuko wamadzi, nabwerera ku mzinda ndipo anati kwa anthu, “Tiyeni mukaone munthu amene wandiwuza ine zilizonse zimene ndinazichita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu?” Iwo anatuluka mʼmudziwo ndi kupita kumene kunali Iye.
Pa nthawi imeneyi ndi kuti ophunzira ake akumukakamiza kuti, “Rabi idyani.”
Koma Iye anawawuza kuti, “Ine ndili ndi chakudya choti ndidye chimene inu simukuchidziwa.”
Ndipo ophunzira ake anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi alipo wina amene anamubweretsera Iye chakudya?”
Yesu anati, “Chakudya changa ndikuchita chifuniro cha Iye amene anandituma Ine ndi kumaliza ntchito yake. Kodi inu simunena kuti, ‘Kwatsala miyezi inayi ndipo kenaka kukolola?’ Ine ndikukuwuzani kuti, tsekulani maso anu ndipo muyangʼane mʼminda! Mbewu zacha kale kuti zikololedwe. Ngakhale tsopano amene akukolola akulandira malipiro ake, ndipo akututa mbewu ku moyo wosatha kuti wofesa ndi wokolola asangalale pamodzi. Nʼchifukwa chake mawu akuti, ‘Wina amafesa ndipo wina amakolola’ ndi woona. Ine ndinakutumani kukakolola zimene simunagwirire ntchito. Ena anagwira ntchito yolemetsa ndipo inu mwatuta phindu la ntchito yawo.”
Asamariya Ambiri Akhulupirira
Asamariya ambiri ochokera mʼmudziwo anakhulupirira Iye chifukwa cha umboni wa mayiyo wakuti, “Iye anandiwuza ine zonse ndinazichita.” Choncho Asamariya atabwera kwa Iye, anamuwumiriza Iye kuti akhale nawo, ndipo Iye anakhala nawo masiku awiri. Ndipo chifukwa cha mawu ake, ena ambiri anakhulupirira.
Iwo anati kwa mayiyo, “Ife sitikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha, koma tsopano ife tadzimvera tokha, ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndithu ndi Mpulumutsi wa dziko lapansi.”
Yesu Achiritsa Mwana wa Nduna ya Mfumu
Patatha masiku awiri Iye anachoka napita ku Galileya. (Tsopano Yesu mwini ananena kale kuti mneneri salandira ulemu mʼdziko lake). Iye atafika ku Galileya, Agalileya anamulandira. Iwo anali ataona zonse zimene anazichita mu Yerusalemu pa phwando la Paska, pakuti iwonso anali komweko.
Iye anakafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasanduliza madzi kukhala vinyo. Ndipo kumeneko kunali nduna ina ya mfumu imene mwana wake wamwamuna anali chigonere akudwala ku Kaperenawo. Munthu uyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa Iye, namupempha kuti apite akachiritse mwana wakeyo, amene anali pafupi kufa.
Yesu anawawuza iwo kuti, “Anthu inu pokhapokha mutaona zizindikiro zodabwitsa, simudzakhulupirira.”
Nduna ya mfumuyo inati, “Ambuye tiyeni mwana wanga asanafe.”
Yesu anayankha kuti, “Pita. Mwana wako adzakhala ndi moyo.”
Munthuyo anakhulupirira mawu a Yesu ndipo ananyamuka. Iye ali pa njira, antchito ake anakumana naye, namuwuza kuti mwana wanu uja wachira. Iye atafunsa kuti ndi nthawi yanji imene mwana wake anapeza bwino, iwo anati kwa iye, “Malungo anamusiya iye dzulo pa ora lachisanu ndi chiwiri.”
Ndipo bamboyo anazindikira kuti iyi inali nthawi yomweyo imene Yesu anati kwa iye, “Mwana wako adzakhala ndi moyo.” Choncho iye ndi onse a pa banja lake anakhulupirira.
Ichi ndiye chinali chizindikiro chodabwitsa chachiwiri chimene Yesu anachita atafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya.
Yesu Achiritsa Munthu pa Sabata
Patapita nthawi Yesu anakwera kupita ku Yerusalemu ku phwando la Ayuda. Ndipo ku Yerusalemuko pafupi ndi chipata cha Nkhosa kuli dziwe limene mʼChihebri limatchedwa Betisaida ndipo ndi lozunguliridwa ndi makumbi asanu. Mʼmenemo munkagonamo gulu lalikulu la anthu odwala, osaona, olumala ndi ofa ziwalo. Pakuti nthawi zina mngelo wa Ambuye ankatsikira mʼdziwemo nʼkuvundula madziwo. Woyamba kulowamo madzi atavundulidwa, ankachira ngakhale akhale ndi nthenda yanji. Mmodzi wa amene anali pamenepo anali atadwala zaka 38. Yesu atamuona ali chigonere, nadziwa kuti anakhala chotero kwa nthawi yayitali, anamufunsa iye kuti, “Kodi ukufuna kuchira?”
Wodwalayo anayankha kuti, “Ambuye, ndilibe wina aliyense woti angandithandize kulowa mʼdziwe pamene madzi avundulidwa. Pamene ndikuyesera kuti ndilowemo, wina amalowamo ine ndisanalowemo.”
Ndipo Yesu anati kwa iye, “Imirira! Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.” Nthawi yomweyo munthuyo anachiritsidwa. Iye ananyamula mphasa yake nayamba kuyenda.
Tsiku limene izi zinachitika linali la Sabata. Ndipo Ayuda anati kwa munthu amene anachiritsidwayo, “Lero ndi la Sabata; lamulo silikulola iwe kunyamula mphasa yako.”
Koma iye anayankha kuti, “Munthu amene wandichiritsa anati kwa ine, ‘Nyamula mphasa yako yamba kuyenda.’ ”
Pamenepo anamufunsa iye kuti, “Kodi munthu ameneyo ndani amene wakuwuza kuti, ‘Nyamula mphasa yako ndipo yenda?’ ”
Munthu amene anachiritsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, pakuti Yesu anangolowera mʼgulu la anthu ndi kupita.
Patapita nthawi Yesu anamupeza ku Nyumba ya Mulungu ndipo anati kwa iye, “Taona uli bwino tsopano. Usakachimwenso kuti choyipa choposa ichi chingakugwere.” Munthu uja anachoka ndi kukawawuza Ayuda kuti anali Yesu amene anamuchiritsa iye.
Yesu Adziwulula kuti ndi Mwana wa Mulungu
Ndipo popeza Yesu amachita zinthu izi tsiku la Sabata, Ayuda anayamba kumulondalonda. Yesu anawawuza kuti, “Atate anga amagwira ntchito nthawi zonse mpaka lero lino, ndipo Inenso ndili pa ntchito.” Chifukwa cha ichi Ayuda anawirikiza kufuna kumupha; osati chifukwa chakuswa Sabata kokha komanso chifukwa ankanena kuti Mulungu ndi Atate ake, nadziyesa Iye wofanana ndi Mulungu.
Yesu anawapatsa yankho ili: “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Mwana sangathe kuchita kanthu pa Iye yekha. Iye amachita zokhazo zimene amaona Atate ake akuchita, chifukwa chilichonse chimene Atate amachita Mwana amachitanso. Pakuti Atate amakonda Mwana, amamuonetsa zonse zimene Iwo amachita. Inde, Atate adzamuonetsa zinthu zazikulu kuposa zimenezi ndipo mudzadabwa. Pakuti monga Atate amaukitsa akufa nawapatsa moyo, momwemonso Mwana amapereka moyo kwa amene Iye akufuna. Komanso, Atate saweruza aliyense koma wapereka kwa Mwana ulamuliro woweruzawo, kuti aliyense alemekeze Mwanayo monga momwe amalemekezera Atate. Munthu amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma Mwanayo.
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene amamva mawu anga ndi kukhulupirira Iye amene ananditumiza Ine, ali ndi moyo wosatha ndipo sadzaweruzidwa. Iye wachoka mu imfa ndipo walowa mʼmoyo. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti nthawi ikubwera ndipo yafika kale tsopano, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo iwo amene amva adzakhala ndi moyo. Pakuti monga Atate ali gwero la moyo, momwemonso anapereka mphamvu zopereka moyo mwa Mwana. Ndipo wamupatsa Iye ulamuliro woweruza chifukwa ndi Mwana wa Munthu.
“Musadabwe ndi zimenezi. Pakuti nthawi ikubwera pamene onse amene ali mʼmanda adzamva mawu ake ndi kutuluka. Iwo amene anachita zabwino adzauka ndi kupita ku moyo wosatha ndipo amene anachita zoyipa adzauka ndi kupita ku chilango chamuyaya. Pakuti sindingathe kuchita kena kalikonse pa ndekha. Ine ndimaweruza molingana ndi zomwe Mulungu wandiwuza ndipo kuweruza kwanga ndi kolungama. Ine sindifuna kudzikondweretsa ndekha koma Iye amene anandituma.
Maumboni Onena za Yesu
“Ngati ndidzichitira umboni ndekha, umboni wanga si woona. Alipo wina amene amandichitira umboni wabwino. Ine ndikudziwa kuti umboni wake wonena za Ine ndi woona.
“Inu munatumiza amithenga kwa Yohane ndipo iye anachitira umboni choona. Sikuti Ine ndikudalira umboni wa munthu; koma ndikunena zimenezi kuti mupulumutsidwe. Yohane anali ngati nyale imene imayaka ndi kuwala, ndipo inu kwa kanthawi munasankha kusangalala ndi kuwala kwakeko.
“Koma Ine ndili ndi umboni woposa uja wa Yohane. Pakuti ntchito imene Atate andipatsa kuti ndiyikwaniritse ndi imene ndikugwira, ndipo ikundichitira umboni kuti Atate andituma Ine. Ndipo Atate amene anandituma Ine, Iye mwini wandichitira umboni. Inu simunamvepo mawu ake kapena kuona maonekedwe ake, kapena mawu ake kukhala mwa inu, pakuti simukhulupirira Iye amene anamutuma. Inu mumasanthula malemba chifukwa mumaganiza kuti mʼmalembamo muli moyo wosatha. Awa ndi malemba amene akundichitira umboni. Koma inu mukukana kubwera kwa Ine kuti mukhale ndi moyo.
“Ine sindilandira ulemu kuchokera kwa anthu koma Ine ndikukudziwani. Ndikudziwa kuti mʼmitima mwanu mulibe chikondi cha Mulungu. Ine ndabwera mʼdzina la Atate anga, ndipo inu simukundirandira Ine; koma wina wake akabwera mʼdzina la iye mwini, inu mudzamulandira. Kodi inu mudzakhulupirira bwanji ngati mumapatsana ulemu wina ndi mnzake, ndipo simufuna kulandira ulemu kuchokera kwa Mulungu yekhayo?
“Koma inu musaganize kuti Ine ndidzakunenezani kwa Atate. Wokunenezani ndi Mose, amene inu mwayikapo chiyembekezo chanu. Ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso Ine, pakuti iye analemba za Ine. Koma ngati simukhulupirira zimene iye analemba, mudzakhulupirira bwanji zimene Ine ndikunena?”
Yesu Adyetsa Anthu 5,000
Nthawi ina zitatha izi, Yesu anawolokera ku gombe la kutali la nyanja ya Galileya (iyi ndi nyanja ya Tiberiya), ndipo gulu lalikulu la anthu linamutsata Iye chifukwa linaona zizindikiro zodabwitsa zimene anazichita pa odwala. Kenaka Yesu anakwera pa phiri nakhala pansi ndi ophunzira ake. Tsopano phwando la Paska la Ayuda linali pafupi.
Yesu atakweza maso ndi kuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa Iye, anati kwa Filipo, “Kodi tingagule kuti buledi kuti anthu awa adye?” Iye anafunsa izi kumuyesa chabe, pakuti Iye ankadziwa chimene ankayenera kuchita.
Filipo anamuyankha Iye kuti, “Malipiro a miyezi isanu ndi itatu sangathe kugula buledi okwanira aliyense kuti adye!”
Mmodzi wa ophunzira ake, Andreya, mʼbale wa Simoni Petro, anati, “Pano pali mnyamata amene ali ndi buledi musanu wabarele ndi tinsomba tiwiri, kodi zingakwane onsewa?”
Yesu anati, “Awuzeni anthuwa akhale pansi.” Pamalo pamenepa panali udzu wambiri ndipo amuna amene anakhala pansi anali osachepera 5,000. Kenaka Yesu anatenga bulediyo, atayamika anagawira iwo amene anakhala pansi, chimodzimodzinso nsombazo monga momwe iwo anafunira.
Ndipo atakhuta, Iye anati kwa ophunzira ake, “Tolani zotsala kuti pasawonongeke kanthu.” Choncho iwo anasonkhanitsa makombo nadzaza madengu khumi ndi awiri.
Pambuyo pake anthu ataona chizindikiro chodabwitsa chimene Yesu anachita, iwo anati, “Zoonadi uyu ndi Mneneri wakudzayo mʼdziko la pansi.” Yesu atadziwa kuti iwo amafuna kubwera kudzamuwumiriza kuti akhale mfumu, anachoka napita ku phiri pa yekha.
Yesu Ayenda pa Madzi
Pofika madzulo, ophunzira ake anatsikira ku nyanja, kumene iwo analowa mʼbwato ndi kuyamba kuwoloka nyanja kupita ku Kaperenawo. Tsopano kunali kutada ndipo Yesu anali asanabwerere kwa iwo. Mphepo yamphamvu inawomba ndipo nyanja inalusa. Iwo atayenda makilomita asanu kapena asanu ndi limodzi, anaona Yesu akuyandikira bwatolo, akuyenda pa madzi; ndipo anachita mantha. Koma Iye anawawuza kuti, “Ndine, musaope.” Ndipo iwo analola kumutenga mʼbwatomo, nthawi yomweyo bwatolo linafika ku gombe la nyanja kumene ankapita.
Pa tsiku lotsatira gulu la anthu limene linatsala kumbali ina yanyanjayo linaona kuti panali bwato limodzi lokha, ndipo kuti Yesu sanalowe mʼbwatomo pamodzi ndi ophunzira ake, koma kuti ophunzirawo anapita okha. Kenaka mabwato ena ochokera ku Tiberiya anafika pafupi ndi pamalo pamene anthu anadya buledi Ambuye atayamika. Nthawi yomwe gulu la anthu linaona kuti Yesu kapena ophunzira ake sanali pamenepo, ilo linalowanso mʼmabwatowo ndi kupita ku Kaperenawo kukamufunafuna Yesu.
Yesu Chakudya Chamoyo
Atamupeza mbali ina ya nyanjayo, iwo anamufunsa Iye kuti, “Rabi, mwafika nthawi yanji kuno?”
Yesu anawayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mukundifuna, osati chifukwa munaona zizindikiro zodabwitsa koma chifukwa munadya chakudya ndi kukhuta. Gwirani ntchito, osati chifukwa cha chakudya chimene chimawonongeka koma chifukwa cha chakudya chimene sichiwonongeka mpaka ku moyo wosatha, chimene Mwana wa Munthu adzakupatsani. Mulungu Atate anamusindikiza chizindikiro chomuvomereza.”
Kenaka anamufunsa Iye kuti, “Kodi tichite chiyani kuti tigwire ntchito za Mulungu?”
Yesu anayankha kuti, “Ntchito ya Mulungu ndi iyi: Kukhulupirira Iye amene anamutuma.”
Choncho iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi mudzatipatsa chizindikiro chodabwitsa chotani kuti ife tichione ndi kukhulupirira Inu? Kodi mudzachita chiyani? Makolo athu akale anadya mana mʼchipululu; monga zalembedwa: ‘anawapatsa buledi wochokera kumwamba kuti adye.’ ”
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti si Mose amene ankakupatsani chakudya chochokera kumwamba, koma ndi Atate anga amene ankakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. Pakuti chakudya cha Mulungu ndi Iye amene wabwera kuchokera kumwamba ndi kupereka moyo ku dziko la pansi.”
Iwo anati, “Ambuye, kuyambira tsopano muzitipatsa buledi ameneyu.”
Kenaka Yesu ananenetsa kuti, “Ine ndine chakudya chamoyo. Iye amene abwera kwa Ine sadzamva njala, ndipo iye amene akhulupirira Ine sadzamva ludzu. Monga ndakuwuzani kale, ngakhale kuti mwandiona simukukhulupirirabe. Zonse zimene Atate andipatsa zidzabwera kwa Ine, ndipo aliyense amene adzabwera kwa Ine sindidzamutaya kunja. Pakuti Ine ndinatsika kuchokera kumwamba osati kudzachita chifuniro changa koma cha Iye amene anandituma Ine. Ndipo chifuniro cha Iye amene anandituma Ine nʼchakuti ndisatayepo ngakhale ndi mmodzi yemwe mwa onse amene Iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti chifuniro cha Atate anga ndi chakuti aliyense amene aona Mwanayo namukhulupirira akhale ndi moyo wosatha, ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza.”
Pamenepo Ayuda anayamba kungʼungʼudza chifukwa anati, “Ine ndine chakudya chotsika kuchokera kumwamba.” Iwo anati, “Kodi uyu si Yesu, mwana wa Yosefe, amene abambo ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga Iyeyu akunena bwanji kuti, ‘Ine ndinatsika kuchokera kumwamba?’ ”
Yesu anayankha kuti, “Musangʼungʼudze pakati panu.” Palibe munthu amene angabwere kwa Ine, ngati Atate amene anandituma Ine samubweretsa. Ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Aneneri analemba kuti, “Onse adzaphunzitsidwa ndi Mulungu! Aliyense amene amamva Atate ndi kuphunzira kwa Iye amabwera kwa Ine. Palibe amene anaona Atate koma yekhayo amene achokera kwa Mulungu; yekhayo ndiye anaona Atate. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Iye amene akhulupirira ali nawo moyo wosatha. Ine ndine chakudya chamoyo. Makolo anu akale anadya mana mʼchipululu, komabe anafa. Koma pano pali chakudya chochokera kumwamba, chimene munthu akadya sangafe. Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati munthu adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi zonse. Chakudya chimenechi ndi thupi langa, limene Ine ndidzalipereka kuti anthu pa dziko lapansi akhale ndi moyo.”
Kenaka Ayuda anayamba kutsutsana kwambiri pakati pawo kuti, “Kodi munthu uyu angathe kutipatsa bwanji thupi lake kuti tidye?”
Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti ngati simungadye thupi la Mwana wa Munthu ndi kumwa magazi ake, simungakhale ndi moyo mwa inu. Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga ali ndi moyo wosatha ndipo Ine ndidzamuukitsa kwa akufa pa tsiku lomaliza. Pakuti thupi langa ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. Aliyense amene adya thupi langa ndi kumwa magazi anga amakhala mwa Ine, ndi Ine mwa iye. Monga Atate amoyo anandituma Ine, ndipo ndili ndi moyo chifukwa cha Atatewo, chomwechonso amene adya thupi langa adzakhala ndi moyo chifukwa cha Ine. Ichi ndiye chakudya chimene chinatsika kuchokera kumwamba. Makolo athu akale anadya mana ndi kufa, koma iye amene adya chakudya ichi, adzakhala ndi moyo nthawi yonse.” Iye ankanena izi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge mu Kaperenawo.
Ophunzira Ambiri Aleka Kutsata Yesu
Pakumva izi ambiri a ophunzira ake anati, “Ichi ndi chiphunzitso chovuta. Angachilandire ndani?”
Pozindikira kuti ophunzira ake ankangʼungʼudza, Yesu anawafunsa kuti, “Kodi izi zikukukhumudwitsani? Nanga mutaona Mwana wa Munthu akukwera kupita kumene Iye anali poyamba! Mzimu Woyera apereka moyo, thupi silipindula kanthu. Mawu amene ndayankhula kwa inu ndiwo mzimu ndipo ndi moyo. Komabe alipo ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Pakuti Yesu ankadziwa kuyambira pachiyambi ena mwa iwo amene samakhulupirira ndi amene adzamupereka Iye. Iye anapitiriza kunena kuti, “Ichi ndi chifukwa chake ndinakuwuzani kuti palibe wina angabwere kwa Ine pokhapokha Atate atamuthandiza.”
Kuyambira nthawi imeneyi ophunzira ake ambiri anabwerera ndipo sanamutsatenso Iye.
Yesu anafunsa khumi ndi awiriwo kuti, “Kodi inu mukufuna kuchokanso?”
Simoni Petro anamuyankha Iye kuti, “Ambuye, ife tidzapita kwa yani? Inu muli ndi mawu amoyo wosatha. Ife tikhulupirira ndi kudziwa kuti Inu ndinu Woyerayo wa Mulungu.”
Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi Ine sindinakusankheni inu khumi ndi awiri? Komabe mmodzi wa inu ndi mdierekezi.” (Iye amanena Yudasi, mwana wa Simoni Isikarioti amene ngakhale anali mmodzi mwa khumi ndi awiriwo, anali woti adzamupereka).
Yesu Apita Kuphwando Lamisasa
Zitatha izi Yesu anayendayenda mu Galileya, ndi cholinga chakuti asafike ku Yudeya chifukwa Ayuda kumeneko amadikira kuti amuphe. Koma phwando la Ayuda lamisasa litayandikira, abale a Yesu anati kwa Iye, “Inu muyenera kuchoka kuno ndi kupita ku Yudeya, kuti ophunzira anu akaone zodabwitsa zomwe mumachita. Palibe wina aliyense amene amafuna kukhala wodziwika amachita zinthu mseri. Popeza Inu mukuchita zinthu izi, mudzionetsere nokha ku dziko la pansi.” Pakuti ngakhale abale ake omwe sanamukhulupirire.
Choncho Yesu anawawuza iwo kuti, “Nthawi yanga yoyenera sinafike; kwa inu nthawi ina iliyonse ndi yoyenera. Dziko lapansi silingakudeni inu, koma limandida Ine chifukwa Ine ndimachitira umboni kuti zomwe limachita ndi zoyipa. Inu pitani kuphwando. Ine sindipita tsopano kuphwando ili chifukwa kwa Ine nthawi yoyenera sinafike.” Atanena izi, Iye anakhalabe mu Galileya.
Komabe, abale ake atanyamuka kupita kuphwando, Iye anapitanso, osati moonekera, koma mseri. Tsopano kuphwandoko Ayuda anakamufunafuna ndi kumafunsana kuti, “Kodi munthu ameneyu ali kuti?”
Pakuti pa chigulu cha anthu panali kunongʼona ponseponse za Iye. Ena ankanena kuti, “Iye ndi munthu wabwino.”
Ena ankayankha kuti, “Ayi, Iye amanamiza anthu.” Koma panalibe amene ankanena kalikonse poyera za Iye chifukwa choopa Ayuda.
Yesu Aphunzitsa pa Phwando
Phwando lili pakatikati, Yesu anapita ku bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi kuyamba kuphunzitsa. Ayuda anadabwa ndipo anafunsa kuti, “Kodi munthu uyu nzeru izi anazitenga kuti popanda kuphunzira?”
Yesu anayankha kuti, “Chiphunzitso changa si cha Ine ndekha. Chimachokera kwa Iye amene anandituma. Ngati munthu asankha kuchita chifuniro cha Mulungu, adzazindikira ngati chiphunzitso changa nʼchochokera kwa Mulungu kapena ngati ndi mwa Ine ndekha. Iye amene amayankhula za Iye mwini amatero kuti adzipezere ulemu, koma amene amagwira ntchito kuti amene anamutuma alandire ulemu, ameneyo ndiye munthu woona; mu mtima mwake mulibe chinyengo chilichonse. Kodi Mose sanakupatseni lamulo? Komatu palibe ndi mmodzi yemwe mwa inu amene akusunga lamulo. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha Ine?”
Gulu la anthu linayankha kuti, “Iwe ndiye wagwidwa ndi ziwanda. Ndani akufuna kukupha?”
Yesu anawawuza kuti, “Ine ndinachita chodabwitsa chimodzi ndipo inu mwadabwa. Koma, chifukwa chakuti Mose anakulamulani kuti muzichita mdulidwe (ngakhale kuti sunachokere kwa Mose, koma kwa makolo anu), inuyo mumachita mdulidwe mwana tsiku la Sabata. Tsopano ngati mwana angachite mdulidwe pa Sabata kuti lamulo la Mose lisaswedwe, nʼchifukwa chiyani mukundipsera mtima chifukwa chochiritsa munthu pa Sabata? Musamaweruze potengera maonekedwe chabe, koma weruzani molungama.”
Kodi Yesu ndi Khristu?
Pa nthawi imeneyi anthu ena a ku Yerusalemu anayamba kufunsana kuti, “Kodi uyu si munthu uja akufuna kumuphayu? Uyu ali apa, kuyankhula poyera, ndipo iwo sakunena kanthu kwa Iye. Kodi olamulira atsimikizadi kuti Iye ndi Khristu? Koma ife tikudziwa kumene achokera munthuyu; pamene Khristu adzabwere, palibe amene adzadziwa kumene akuchokera.”
Kenaka Yesu, akuphunzitsabe mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafuwula kuti, “Zoona, mukundidziwa Ine, ndipo mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindili pano mwa Ine ndekha, koma Iye amene anandituma Ine ndi woona. Inu simukumudziwa, koma Ine ndikumudziwa chifukwa ndichokera kwa Iyeyo ndipo ndiye amene anandituma Ine.”
Chifukwa cha izi iwo anayesa kumugwira Iye, koma palibe aliyense amene anayika dzanja lake pa Iye, chifukwa nthawi yake inali isanafike. Komabe, ambiri a mʼchigulucho anamukhulupirira Iye. Iwo anati, “Kodi pamene Khristu abwera, adzachita zizindikiro zodabwitsa zambiri kuposa munthu uyu?”
Afarisi anamva chigulucho chikunongʼona zinthu zotere za Iye. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anatumiza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu kuti akamumange Iye.
Yesu anati, “Ine ndili ndi inu kwa kanthawi kochepa chabe, ndipo kenaka ndizipita kwa Iye amene anandituma Ine. Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza; ndipo kumene Ine ndili inu simungathe kubwera.”
Ayuda anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi munthu uyu akuganizira zoti apite kuti kumene ife sitingathe kumupeza Iye? Kodi Iye adzapita kumene anthu amakhala mobalalikana pakati pa Agriki, ndi kuphunzitsa Agriki? Kodi Iye amatanthauza chiyani pamene anati, ‘Inu mudzandifunafuna koma simudzandipeza,’ ndi ‘Kumene Ine ndili, inu simungathe kubwera?’ ”
Mitsinje ya Madzi Opatsa Moyo
Pa tsiku lomaliza ndi lalikulu kwambiri laphwando, Yesu anayimirira nafuwula nati, “Ngati munthu ali ndi ludzu, abwere kwa Ine kuti adzamwe. Malemba kuti ‘Aliyense amene akhulupirira Ine, mitsinje yamadzi amoyo idzatuluka kuchokera mʼkati mwake.’ ” Ponena izi Iye amatanthauza Mzimu Woyera, amene adzalandire amene amakhulupirira Iye. Pa nthawiyi nʼkuti Mzimu Woyera asanaperekedwe, pakuti Yesu anali asanalemekezedwe.
Pakumva mawu ake, ena a anthuwo anati, “Zoonadi munthu uyu ndi mneneri.”
Ena anati, “Iye ndiye Khristu.”
Komanso ena anafunsa kuti, “Kodi Khristu angachokere bwanji ku Galileya? Kodi Malemba samanena kuti Khristu adzachokera mʼbanja la Davide, ndi ku Betelehemu mu mzinda umene Davide anakhalamo?” Kotero anthu anagawikana chifukwa cha Yesu. Ena anafuna kumugwira Iye, koma palibe amene anayika dzanja pa Iye.
Kusakhulupirira kwa Atsogoleri a Ayuda
Pomaliza asilikali a mʼNyumba ya Mulungu anabwerera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi amene anawafunsa iwo kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani simunamugwire Iye?”
Asilikali aja anati, “Palibe wina amene anayankhula ngati Munthu ameneyo nʼkale lonse.”
Afarisi anawadzudzula nati, “Kodi mukutanthauza kuti Iye anakunamizani inunso?” “Kodi alipo ena a olamulira kapena a Afarisi, anamukhulupirira Iye? Ayi! Koma gulu limene silidziwa malamulo ndi lotembereredwa.”
Nekodimo, amene anapita kwa Yesu poyamba paja ndipo anali mmodzi wa iwo, anafunsa kuti, “Kodi lamulo lathu limatsutsa munthu popanda kumva mbali yake kuti tipeze chimene wachita?”
Iwo anayankha kuti, “Kodi ndiwenso wochokera ku Galileya? Tayangʼananso, ndipo udzapeza kuti mneneri sachokera ku Galileya.”
[Mipukutu yoyambirira ndi maumboni akale mulibe 7:53 mpaka 8:11]
Za Mkazi Wachigololo
Kenaka onse anachoka, napita kwawo.
Koma Yesu anapita ku phiri la Olivi. Mmamawa Iye anaonekeranso ku Nyumba ya Mulungu kumene anthu onse anamuzungulira ndipo Iye anakhala pansi nawaphunzitsa. Aphunzitsi amalamulo ndi Afarisi anabweretsa mkazi amene anagwidwa akuchita chigololo. Iwo anamuyimiritsa patsogolo pa anthu ndipo anati kwa Yesu, “Aphunzitsi, mkazi uyu tinamugwira akuchita chigololo. Mʼmalamulo a Mose anatilamulira kuti akazi otere tiwagende ndi miyala. Tsopano Inu mukuti chiyani?” Iwo anagwiritsa ntchito funsoli ngati msampha, ndi cholinga choti apeze chifukwa cha kumuneneza Iye.
Koma Yesu anawerama pansi ndi kuyamba kulemba pa dothi ndi chala chake. Pamene iwo anapitirira kumufunsa, Iye anaweramuka ndipo anawawuza kuti, “Ngati wina wa inu alipo wopanda tchimo, ayambe iyeyo kumugenda ndi miyala mkaziyu.” Iye anaweramanso pansi ndi kulemba pa dothi.
Iwo atamva izi anayamba kuchoka mmodzimmodzi, akuluakulu poyamba, mpaka Yesu anatsala yekha ndi mkaziyo atayimirira pomwepo. Yesu anaweramuka ndipo anamufunsa iye kuti, “Akuluakulu aja ali kuti? Kodi palibe amene wakutsutsa?”
Iye anati, “Ambuye, palibe ndi mmodzi yemwe.”
“Inenso sindikukutsutsa iwe. Pita kuyambira tsopano usakachimwenso.”
Za Umboni wa Yesu
Yesu atayankhulanso kwa anthu, anati, “Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi. Aliyense amene anditsata Ine sadzayenda mu mdima, koma adzakhala ndi kuwala kotsogolera anthu ku moyo.”
Afarisi anamutsutsa Iye nati, “Iwe ukudzichitira umboni wa Iwe mwini, umboni wako siwoona.”
Yesu anayankha kuti, “Ngakhale Ine ndidzichitire umboni, umboni wangawu ndi woona, pakuti Ine ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa ndi pangʼono pomwe kumene ndinachokera kapena kumene ndikupita. Inu mumaweruza potsata maganizo a anthu chabe. Ine sindiweruza munthu wina aliyense. Koma Ine ndikati ndiweruze, ndimaweruza molondola, chifukwa Ine sindili ndekha koma ndili ndi Atate amene anandituma. Mʼmalamulo anu munalembedwa kuti umboni wa anthu awiri ndi wovomerezeka. Ine ndikudzichitira ndekha umboni; ndipo mboni inanso ndi Atate amene anandituma.”
Kenaka iwo anamufunsa Iye kuti, “Kodi Atate anuwo ali kuti?”
Yesu anayankha kuti, “Inu simundidziwa Ine. Atate anganso simuwadziwa. Mukanandidziwa Ine, mukanawadziwanso Atate anga.” Iye anayankhula mawu awa pamene amaphunzitsa Nyumba ya Mulungu pafupi ndi malo amene amaponyapo zopereka. Komabe palibe amene anamugwira Iye, chifukwa nthawi yake inali isanakwane.
Mkangano Woti Yesu Ndani
Kenakanso Yesu anawawuza kuti, “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa muli mʼmachimo anu. Kumene ndikupita, inu simungabwereko.”
Izi zinachititsa Ayuda kufunsa kuti, “Kodi adzadzipha yekha? Kodi ndicho chifukwa chake akuti, ‘Kumene ndikupita, inu simungabwereko?’ ”
Koma Iye anapitiriza kuti, “Inu ndi ochokera pansi pano. Ine ndine wochokera kumwamba. Inu ndinu anthu a dziko la pansi. Ine sindine wa dziko lapansi lino. Ine ndinakuwuzani kuti mudzafera mʼmachimo anu ngati simukhulupirira kuti Ine Ndine. Ndithu inu mudzafera mʼmachimo anu.”
Iwo anafunsa kuti, “Ndinu ndani?”
Yesu anayankha kuti, “Monga Ine ndakhala ndikunena nthawi yonseyi, ndili ndi zambiri zoti ndinene zoweruza inu. Koma Iye amene anandituma ndi woona, ndipo chimene Ine ndamva kuchokera kwa Iye, ndi chimene ndimaliwuza dziko lapansi.”
Iwo sanazindikire kuti Iye amawawuza za Atate ake. Choncho Yesu anati, “Inu mukadzapachika Mwana wa Munthu, pamenepo mudzadziwa kuti Ine Ndine. Mudzadziwa kuti sindichita kalikonse pa Ine ndekha koma ndimayankhula zokhazo zimene Atate anandiphunzitsa. Iye amene anandituma Ine ali nane pamodzi. Iye sanandisiye ndekha popeza nthawi zonse ndimachita zomwe zimamukondweretsa Iye.” Pamene Iye ankayankhula zimenezi, ambiri anamukhulupirira.
Ana a Abrahamu
Kwa Ayuda amene anamukhulupirira, Yesu anati, “Ngati inu mutsatira chiphunzitso changa, ndithu ndinu ophunzira anga. Tsono mudzadziwa choonadi, ndipo choonadicho chidzakumasulani.”
Iwo anamuyankha Iye kuti, “Ife ndife zidzukulu za Abrahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a wina aliyense. Kodi mukunena bwanji kuti, ‘Ife tidzamasulidwa?’ ”
Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wochita tchimo ndi kapolo wa tchimolo. Pajatu kapolo alibe malo wokhazikika mʼbanja, koma mwana ndi wa mʼbanjamo nthawi zonse. Nʼchifukwa chake ngati Mwana adzakumasulani, mudzakhala mfulu ndithu. Ine ndikudziwa kuti inu ndinu zidzukulu za Abrahamu. Chonsecho inu mwakonzeka kundipha Ine, chifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. Ine ndikukuwuzani zimene ndaziona pamaso pa Atate, ndipo inu mukuchita zimene mwazimva kwa abambo anu.”
Iwo anayankha kuti, “Ife abambo athu ndi Abrahamu.”
Yesu anati, “Inu mukanakhala ana a Abrahamu, bwenzi mukuchita zinthu zimene Abrahamuyo ankachita. Koma mmene zililimu, inu mwatsimikiza kundipha Ine, munthu amene ndinakuwuzani choonadi chimene Ine ndinachimva kuchokera kwa Mulungu. Abrahamu sanachite zinthu zoterezi. Inu mukuchita zinthu zimene abambo anu amachita.”
Iwo anatsutsa kuti, “Ife si ana amʼchigololo, Atate amene tili nawo ndi Mulungu yekha.”
Ana a Mdierekezi
Yesu anawawuza kuti, “Mulungu akanakhala Atate anu, inu mukanandikonda Ine, pakuti Ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo tsopano ndili pano. Ine sindinabwere mwa Ine ndekha. Nʼchifukwa chiyani simukumvetsetsa mawu anga? Chifukwa chake nʼchakuti simungathe kumva zoyankhula zanga. Inu ndinu ana a mdierekezi. Iye ndiye abambo anu ndipo mukufuna kuchita zimene abambo anuwo amakhumba. Iye anali wakupha kuyambira pachiyambi, sanasunge choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene Iye anena bodza, amayankhula chiyankhulo chobadwa nacho, popeza ndi wabodza ndipo ndi bambo wa mabodza. Koma chifukwa ndikuwuzani choonadi, inu simukundikhulupirira Ine! Ndani mwa inu angatsimikize kuti ndine wochimwa? Ngati Ine ndikunena choonadi, nʼchifukwa chiyani simukundikhulupirira? Munthu wochokera kwa Mulungu amamva zimene Mulungu amanena. Chifukwa chimene simumvera nʼchakuti, inuyo sindinu ochokera kwa Mulungu.”
Zomwe Yesu Ananena za lye Mwini
Ayuda anamuyankha Iye kuti, “Kodi ife sitikulondola ponena kuti Inu ndi Msamariya ndi wogwidwa ndi chiwanda?”
Yesu anati, “Ine sindinagwidwe ndi chiwanda, koma ndimalemekeza Atate anga, koma inu mukundinyoza. Ine sindidzifunira ndekha ulemu; koma alipo wina amene amandifunira, ndipo Iyeyo ndiye woweruza. Ine ndikukuwuzani choonadi, munthu akasunga mawu anga, sadzafa konse.”
Pamenepo Ayuda anafuwula kuti, “Tsopano ife tadziwadi kuti Inu ndi wogwidwa ndi chiwanda! Abrahamu anafa ndiponso aneneri, koma Inu mukunena kuti, ‘Ngati munthu asunga mawu anga, sadzafa.’ Kodi ndinu wa mkulu kuposa abambo athu Abrahamu? Iye anafa, ndiponso aneneri onse. Inu mukuganiza kuti ndinu yani?”
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndidzilemekeza ndekha, ulemu wangawo ndi wosatanthauza kanthu. Atate anga amene inu mukuti ndi Mulungu wanu, ndiye amene amandilemekeza Ine. Ngakhale kuti inuyo simukumudziwa, Ineyo ndikumudziwa. Ngati Ine nditanena kuti sindikumudziwa, Ineyo nditha kukhala wabodza ngati inuyo, koma Ine ndimamudziwa ndipo ndimasunga mawu ake. Abambo anu Abrahamu anakondwera poyembekezera kubwera kwanga. Iwo anandiona ndipo anasangalala.”
Ayuda anati kwa Iye, “Inu sumunafike nʼkomwe zaka makumi asanu, ndipo mukuti munamuona Abrahamu!”
Yesu anayankha kuti, “Ine ndikukuwuzani choonadi, Abrahamu asanabadwe, Ine Ndine!” Pamenepo iwo anatola miyala kuti amugende, koma Yesu anabisala, nachoka mozemba mʼNyumba ya Mulungu.
Yesu Achiritsa Munthu Wosaona Chibadwire
Iye akuyendabe, anaona munthu wosaona chibadwire. Ophunzira ake anamufunsa Iye kuti, “Rabi anachimwa ndani, munthuyu kapena makolo ake, kuti iye abadwe wosaona?”
Yesu anayankha kuti, “Sikuti iyeyu anachimwa kapena makolo ake, koma izi zinachitika kuti Mulungu aonetse ntchito zake mwa iyeyu. Ife tiyenera kugwira ntchito za Iye amene anandituma kukanali masana. Usiku ukubwera, pamene wina aliyense sadzagwira ntchito. Pamene Ine ndili mʼdziko lapansi, Ine ndine kuwunika kwa dziko lapansi.”
Atanena izi, Iye anathira malovu pansi ndi kukanda dothi, napaka matopewo mʼmaso a munthuyo. Yesu anamuwuza iye kuti, “Pita kasambe mʼdziwe la Siloamu” (mawu awa akutanthauza Wotumidwa). Choncho munthuyo anapita ndi kukasamba ndipo anabwerako akupenya.
Anzake ndi iwo amene anamuona iye poyamba akupempha anafunsa kuti, “Kodi uyu si munthu amene amapemphapempha uja?” Ena ananena kuti anali yemweyo.
Ena anati, “Ayi, sakuoneka ngati yemweyo.”
Koma iye mwini ananenetsa kuti, “Munthuyo ndine.”
Iwo anafunsitsa kuti, “Kodi nanga maso ako anatsekuka bwanji?”
Iye anayankha kuti, “Munthu wina wotchedwa Yesu anakanda dothi ndi kupaka mʼmaso anga. Iye anandiwuza kuti ndipite ku Siloamu ndi kukasamba. Choncho ndinapita kukasamba, ndipo ndikuona.”
Iwo anamufunsa iye kuti, “Ali kuti munthu ameneyu?”
Iye anati, “Ine sindikudziwa.”
Afarisi Afufuza za Kuchiritsidwa Kwake
Iwo anabwera naye munthu amene poyamba anali wosaona kwa Afarisi. Tsono linali la Sabata tsiku limene Yesu anakanda dothi ndi kutsekula maso a munthuyu. Choncho Afarisi anamufunsanso iye momwe analandirira kuona kwake. Munthuyo anayankha kuti, “Iye anapaka matope mʼmaso anga, ndipo ine ndinakasamba, ndipo ndikuona.”
Ena a Afarisi anati, “Munthu uyu siwochokera kwa Mulungu, pakuti sasunga Sabata.”
Koma enanso anafunsa kuti, “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro zodabwitsa ngati izi?” Choncho iwo anagawanika.
Pomaliza iwo anatembenukiranso kwa munthu amene anali wosaona uja nati, “Kodi iwe unena chiyani za Iye poti ndi maso ako amene watsekula?”
Munthuyo anayankha kuti, “Iye ndi mneneri.”
Ayuda sanakhulupirirebe kuti iye anali wosaona ndi kuti anayamba kuona kufikira atayitana makolo ake. Iwo anafunsa kuti, “Kodi uyu ndi mwana wanu? Kodi iyeyu ndi amene mukunena kuti anabadwa wosaona? Nanga zikutheka bwanji kuti akuona?”
Makolo anayankha kuti, “Ife tikudziwa kuti ndi mwana wathu, ndipo tikudziwa kuti anabadwa wosaona. Koma sitidziwa zimene zachitika kuti tsopano azipenya. Amenenso wamupenyetsa sitikumudziwa. Mufunseni ndi wamkulu; iye adziyankhira yekha.” Makolo ake ananena izi chifukwa amaopa Ayuda, popeza Ayuda anatsimikiza kale kuti aliyense amene adzamuvomereza Yesu kuti anali Khristu adzatulutsidwa mʼsunagoge. Ichi ndi chifukwa chake makolo ake anati, “Mufunseni iye ndi wamkulu.”
Iwo anamuyitanitsa kachiwiri munthu amene anali wosaonayo. Iwo anati, “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthu uyu ndi wochimwa.”
Iye anayankha kuti, “Zakuti Iye ndi wochimwa kapena ayi, ine sindikudziwa. Ine ndikudziwa chinthu chimodzi. Ndinali wosaona koma tsopano ndikuona!”
Kenaka anamufunsa kuti, “Kodi Iye anachita chiyani kwa iwe? Iye anatsekula motani maso ako?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kale ndipo inu simunamvetsetse. Chifukwa chiyani mukufuna mumvenso? Mukufuna kuti inu mukhale ophunzira akenso?”
Pamenepo anamunyoza ndipo anati, “Iwe ndiye ophunzira wa munthuyu! Ife ndife ophunzira a Mose! Ife tikudziwa kuti Mulungu anayankhula kwa Mose, koma za munthu uyu, ife sitikudziwa ngakhale kumene akuchokera.”
Munthuyo anayankha kuti, “Tsopano izi ndi zodabwitsa! Inu simukudziwa kumene akuchokera, komabe iye watsekula maso anga. Ife tikudziwa kuti Mulungu samvera wochimwa. Iye amamvera munthu woopa Mulungu amene amachita chifuniro chake. Palibe amene anamvapo za kutsekula maso a munthu wobadwa wosaona. Ngati munthu uyu akanakhala wosachokera kwa Mulungu, palibe chimene Iye akanachita.”
Pamenepo anayankha kuti, “Iwe unabadwa mu uchimo kotheratu; bwanji ukuyesa kutiphunzitsa ife!” Ndipo anamutulutsa kunja.
Kusaona kwa Uzimu
Yesu anamva kuti anamutulutsa kunja ndipo pamene anamupeza anati, “Kodi ukukhulupirira Mwana wa Munthu?”
Munthuyo anafunsa kuti, “Kodi, Ambuye, ameneyo ndi ndani? Ndiwuzeni kuti ndimukhulupirire Iye?”
Yesu anati, “Iwe wamuona tsopano. Zoonadi ndiye amene akuyankhula nawe.”
Pamenepo munthuyo anati, “Ambuye, ndikukhulupirira,” ndipo anamulambira Iye.
Yesu anati, “Ndinabwera pansi pano kudzaweruza kuti osaona aone ndi openya asaone.”
Afarisi ena amene anali pafupi naye anamva akunena izi ndipo anafunsa kuti, “Chiyani? Kodi ndife osaonanso?”
Yesu anati, “Mukanakhala osaona, simukanachimwa; koma tsopano popeza mukuti mumaona, ndinu ochimwabe.”
Mʼbusa Wabwino ndi Nkhosa Zake
“Zoonadi, Ine ndikukuwuzani inu Afarisi, kuti munthu amene salowera pa khomo mʼkhola la nkhosa, koma amalowera pena pake ndi wakuba ndi wachifwamba. Munthu amene amalowera pa khomo ndi mʼbusa wankhosazo. Mlonda amamutsekulira khomo, ndipo nkhosa zimamvera mawu ake. Iye amaziyitana mayina nkhosa zakezo, nazitulutsa. Akazitulutsa nkhosa zake zonse, iye amazitsogolera, ndipo nkhosa zakezo zimamutsata chifukwa zimadziwa mawu ake. Koma nkhosazo sizidzatsatira mlendo. Izo zidzamuthawa chifukwa sizizindikira mawu a mlendo.” Yesu ananena mawu ophiphiritsawa, koma Afarisi sanazindikire zimene ankawawuza.
Choncho Yesu anatinso, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti Ine ndine khomo la nkhosa. Onse amene anadza ndisanabwere Ine ndi akuba ndi achifwamba, ndipo nkhosa sizinawamvere. Ine ndine khomo, aliyense amene alowa kudzera mwa Ine adzapulumuka. Iye adzalowa ndi kutuluka ndi kupeza msipu. Mbala sibwera chabe koma kuti idzabe, kupha ndi kuwononga. Ine ndabwera kuti iwo akhale ndi moyo, ndi kukhala nawo wochuluka.
“Ine ndine Mʼbusa wabwino. Mʼbusa wabwino amataya moyo wake chifukwa cha nkhosa zake. Wantchito ndi mʼbusa amene nkhosazo si zake. Choncho, pamene aona mmbulu ukubwera, iye amazisiya nkhosazo ndi kuthawa. Ndipo mmbulu umagwira nkhosazo ndikuzibalalitsa. Munthuyo amathawa chifukwa ndi wantchito ndipo sasamalira chilichonse cha nkhosazo.
“Ine ndine mʼbusa wabwino. Ine ndimazidziwa nkhosa zanga ndipo nkhosa zangazo zimandidziwa, monga momwe Atate amandidziwa Ine, ndiponso Ine kudziwira Atatewo. Ndimapereka moyo wanga chifukwa cha nkhosa. Ine ndili ndi nkhosa zina zimene sizili za gulu ili. Ine ndiyenera kuzibweretsanso. Izonso zidzamvera mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi mʼbusa mmodzi. Nʼchifukwa chake Atate anga amandikonda, popeza Ine ndikupereka moyo wanga kuti ndiwutengenso. Palibe amene angawuchotse mwa Ine, koma ndikuwupereka mwakufuna kwanga. Ine ndili ndi ulamuliro wa kuwupereka ndi ulamuliro wakuwutenganso. Lamulo ili ndinalandira kwa Atate anga.”
Pa mawu awa Ayuda anagawikananso. Ambiri a iwo anati, “Iye ndi wogwidwa ndi ziwanda ndi wamisala. Chifukwa chiyani mukumvera Iye?”
Koma ena anati, “Awa si mawu a munthu wogwidwa ndi ziwanda. Kodi ziwanda zingathe bwanji kutsekula maso a wosaona?”
Kusakhulupirira kwa Ayuda
Ku Yerusalemu kunali chikondwerero chokumbukira kupatulidwa kwa Nyumba ya Mulungu. Inali nthawi yozizira, ndipo Yesu ankayenda mʼbwalo la Nyumbayo ku malo a Solomoni. Ayuda anamuzungulira Iye akunena kuti, “Kodi iwe udzazunguza malingaliro athu mpaka liti? Ngati iwe ndi Khristu, tiwuze momveka.”
Yesu anayankha kuti, “Ine ndimakuwuzani, koma inu simukhulupirira. Ntchito zimene ndikuchita mʼdzina la Atate anga zikundichitira umboni, koma inu simukhulupirira chifukwa simuli a gulu lankhosa zanga. Nkhosa zanga zimamva mawu anga, Ine ndimazidziwa, ndipo zimanditsata Ine. Ine ndimazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongeka. Palibe amene adzazikwatula mʼdzanja langa. Atate anga, amene anandipatsa Ine, ndi akulu kuposa onse. Palibe amene angazikwatule mʼdzanja la Atate anga. Ine ndi Atate ndife amodzi.”
Ayuda anatolanso miyala kuti amugende Iye, koma Yesu anawawuza kuti, “Ine ndakuonetsani zinthu zambiri zabwino zodabwitsa kuchokera kwa Atate. Nʼchifukwa chiti mwa izi chimene mukundigendera?”
Ayuda anayankha kuti, “Ife sitikukugenda chifukwa cha izi, koma popeza ukunyoza Mulungu, chifukwa iwe, munthu wamba, ukuti ndiwe Mulungu.”
Yesu anawayankha kuti, “Kodi sizinalembedwa mʼmalamulo anu kuti, ‘Ine ndanena kuti ndinu milungu?’ Ngati anawatcha milungu anthu amene analandira mawu a Mulungu, pajatu Malemba sangasweke, nanga bwanji uyu amene Atate anamuyika padera monga wake weniweni ndi kumutuma ku dziko lapansi? Nanga ndi chifukwa chiyani mukundinena Ine kuti ndikuchita chipongwe? Kodi nʼchifukwa choti ndanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu?’ Musandikhulupirire Ine ngati sindichita ntchito za Atate anga. Koma ngati Ine ndikuchita zimenezi, ngakhale kuti simundikhulupirira, khulupirirani ntchito zodabwitsazo, ndipo mudziwe ndi kuzindikira kuti Atate ali mwa Ine, ndiponso Ine ndili mwa Atate.” Iwo anafuna kumugwiranso koma anawapulumuka mʼmanja mwawo.
Kenaka Yesu anabwereranso kutsidya la mtsinje wa Yorodani kumalo kumene Yohane ankabatiza mʼmasiku akale. Iye anakhala kumeneko ndipo anthu ambiri anabwera kwa Iye. Iwo anati, “Ngakhale kuti Yohane sanachite chizindikiro chodabwitsa, zonse zimene Yohane ananena za munthu uyu zinali zoona.” Ndipo pamalo amenewo ambiri anakhulupirira Yesu.
Imfa ndi Kuukitsidwa kwa Lazaro
Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anadwala. Iye anali wa ku Betaniya, mudzi wa Mariya ndi mchemwali wake Marita. Mariyayo ndi yemwe uja amene anadzoza Ambuye ndi mafuta onunkhira napukuta mapazi ake ndi tsitsi lake. Lazaro wodwalayo anali mlongo wake. Choncho alongo ake anatumiza mawu kwa Yesu kuti, “Ambuye, uja amene Inu mumamukonda akudwala.”
Atamva izi, Yesu anati, “Kudwalako safa nako. Koma akudwala kuti Mulungu alemekezedwe; ndi kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe chifukwa cha matendawo.” Yesu anakonda Marita, mchemwali wake ndi Lazaro. Koma atamva kuti Lazaro akudwala, Iye anakhalabe kumene anali masiku ena awiri.
Kenaka anati kwa ophunzira ake, “Tiyeni tibwerere ku Yudeya.”
Ophunzira akewo anati, “Rabi, posachedwa pomwepa Ayuda anafuna kukugendani ndi miyala, koma Inu mukupitanso komweko?”
Yesu anayankha kuti, “Kodi sipali maora khumi ndi awiri pa tsiku? Munthu amene amayenda masana sapunthwa, popeza akuona chifukwa cha kuwala kwa dziko lapansi. Koma amene akuyenda usiku amapunthwa, chifukwa kuwalako alibe.”
Iye atatha kunena izi, anapitirira kuwawuza iwo kuti, “Bwenzi lathu Lazaro wagona tulo; koma Ine ndikupita kumeneko kukamudzutsa.”
Ophunzira ake anayankha kuti, “Ambuye, ngati wagona adzapeza bwino.” Yesu ankayankhula za imfa yake koma ophunzira ake ankaganiza kuti amanena za tulo chabe.
Ndipo kenaka anawawuza momveka kuti, “Lazaro wamwalira. Ine ndikukondwera chifukwa cha inu kuti kunalibe kumeneko; koma kuti mukakhulupirire tiyeni tipiteko.”
Pamenepo Tomasi, wotchedwa Didimo, anati kwa ophunzira anzake, “Tiyeni nafenso tipite, kuti tikafere naye pamodzi.”
Yesu Atonthoza Alongo a Lazaro
Yesu atafika, anapeza kuti Lazaro anali atagona mʼmanda masiku anayi. Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wosachepera makilomita atatu, ndipo Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza pa imfa ya mʼbale wawo. Pamene Marita anamva kuti Yesu akubwera, anapita kukakumana naye. Koma Mariya anatsala ku nyumba.
Marita anati kwa Yesu, “Ambuye, mukanakhala muli kuno, mlongo wanga sakanamwalira. Koma ine ndikudziwa kuti ngakhale tsopano Mulungu adzakupatsani chilichonse chimene mudzamupempha.”
Yesu anati kwa iye, “Mlongo wako adzauka.”
Marita anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti adzauka pa kuukanso pa tsiku lomaliza.”
Yesu anati kwa iye, “Ine ndine kuuka ndi moyo. Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira adzakhala ndi moyo. Aliyense amene ali ndi moyo ndi kukhulupirira Ine sadzamwalira. Kodi iwe ukukhulupirira izi?”
Marita anamuwuza Iye kuti, “Inde Ambuye, ine ndikukhulupirira kuti ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu, amene abwera mʼdziko lapansi.”
Ndipo iye atanena izi anabwerera ndi kukayitana mchemwali wake Mariya namuyankhula monongʼona pambali, nati, “Aphunzitsi abwera ndipo akukuyitana.” Mariya atamva izi, anayimirira mofulumira napita kwa Iye. Tsopano nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzi, koma anali akanali pa malo pamene Marita anakumana naye. Ayuda amene ankamutonthoza Mariya mʼnyumba, anaona mmene iye anayimira mofulumira ndi kutuluka kunja, iwo anamutsata akuganizira kuti ankapita ku manda kukalirira kumeneko.
Mariya anafika pamalo pamene panali Yesu ndipo atamuona, anagwa pa mapazi ake ndipo anati, “Ambuye mukanakhala muli kuno mlongo wanga sakanamwalira.”
Yesu ataona iye akulira, ndi Ayuda amene anabwera naye akuliranso, anakhudzidwa kwambiri ndi kuvutika mu mzimu. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwamuyika kuti?”
Iwo anayankha kuti, “Ambuye tiyeni mukaone.”
Yesu analira.
Pamenepo Ayuda anati, “Taonani mmene Iye anamukondera Lazaro!”
Koma ena a iwo anati, “Iye amatsekula maso a munthu wosaona, kodi sakanakhoza kuletsa kuti munthu uyu asamwalire?”
Yesu Aukitsa Lazaro
Yesu atakhudzidwanso kwambiri anafika ku manda. Manda akewo anali phanga ndipo anatsekapo ndi mwala. Yesu anati, “Chotsani mwala.”
Marita mlongo wa womwalirayo anati, “Koma Ambuye, nthawi ino wayamba kununkha, pakuti wakhala mʼmenemu masiku anayi.”
Kenaka Yesu anati, “Kodi Ine sindinakuwuze kuti ngati iwe ukhulupirira, udzaona ulemerero wa Mulungu?”
Choncho iwo anachotsa mwalawo. Kenaka Yesu anayangʼana kumwamba ndikuti, “Atate, Ine ndikukuthokozani chifukwa mumandimvera. Ine ndimadziwa kuti Inu mumandimvera nthawi zonse, koma Ine ndanena izi chifukwa cha anthu amene ayima pano, kuti iwo akhulupirire kuti Inu munandituma Ine.”
Yesu atanena izi, Iye anayitana ndi mawu ofuwula kuti, “Lazaro, tuluka!” Munthu womwalirayo anatuluka, womangidwa miyendo ndi manja ndi nsalu za ku manda, ndi nkhope yake yokulungidwa nsalu.
Yesu anawawuza kuti, “Mʼmasuleni, ndipo muloleni apite.”
Ayuda Apangana za Kupha Yesu
Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kudzamuchereza Mariya ndi kuona zimene Yesu anachita anamukhulupirira Iye. Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi ndi kukawawuza zimene Yesu anachita. Kenaka akulu a ansembe ndi Afarisi anayitanitsa msonkhano wa akulu olamulira.
Iwo anafunsa kuti, “Kodi ife tikuchita chiyani? Pano pali munthu uyu akuchita zizindikiro zodabwitsa zambiri. Ngati ife timuleka kuti apitirize chotere, aliyense adzamukhulupirira Iye, ndipo kenaka Aroma adzabwera ndi kudzatenga malo athu pamodzi ndi dziko lathu.”
Kenaka mmodzi wa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anayankhula kuti, “Inu simukudziwa kanthu kalikonse! Inu simukuzindikira kuti kuli bwino kwa inu kuti munthu mmodzi afe mʼmalo mwa anthu kusiyana ndi kuti mtundu wonse uwonongeke.”
Iye sananene izi mwa iye yekha, koma monga mkulu wa ansembe chaka chimenecho ananenera kuti Yesu anayanera kufera mtundu wa Ayuda, ndipo osati mtundu okhawo komanso kwa ana ena a Mulungu onse obalalikana, kuti awabweretse pamodzi ndi kuwapanga kukhala amodzi. Choncho kuyambira tsiku limeneli iwo anakonzekera za kuti amuphe.
Chifukwa cha ichi Yesu sanayendenso moonekera pakati pa Ayuda. Mʼmalo mwake Iye anapita ku chigawo cha kufupi ndi chipululu, ku mudzi wa Efereimu, kumene Iye anakhalako ndi ophunzira ake.
Nthawi ya Paska wa Ayuda itayandikira, ambiri anakwera kupita ku Yerusalemu kuchokera ku madera a ku midzi chifukwa cha mwambo wa kuyeretsedwa Paska asanafike. Iwo anapitiriza kumufunafuna Yesu, ndipo pamene ankayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu anafunsana wina ndi mnzake kuti, “Kodi ukuganiza chiyani? Kodi Iye sabwera konse kuphwando?” Koma akulu a ansembe ndi Afarisi anapereka lamulo kuti ngati wina aliyense adziwe kumene kunali Yesu, iye akawawuze kuti akamugwire.
Mariya Adzoza Mapazi a Yesu
Masiku asanu ndi limodzi Paska asanafike, Yesu anafika ku Betaniya, kumene kumakhala Lazaro, amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. Kumeneko anamukonzera Yesu chakudya cha madzulo. Marita anatumikira pamene Lazaro anali mmodzi wa iwo amene anakhala nawo pa chakudyacho. Kenaka Mariya anatenga botolo la mafuta a nadi, onunkhira bwino kwambiri, amtengowapatali; Iye anadzoza mapazi a Yesu napukuta ndi tsitsi lake. Ndipo nyumba yonse inadzaza ndi fungo lonunkhira bwino la mafutawo.
Koma mmodzi wa ophunzira ake, Yudasi Isikarioti, amene pambuyo pake adzamupereka anati, “Nʼchifukwa chiyani mafuta awa sanagulitsidwe ndipo ndalama zake nʼkuzipereka kwa osauka?” Mafutawo anali a mtengo wa malipiro a chaka chimodzi. Iye sananene izi chifukwa cha kuganizira osauka koma chifukwa anali mbava; ngati wosunga thumba la ndalama, amabamo zomwe ankayikamo.
Yesu anayankha kuti, “Mulekeni. Mafutawa anayenera kusungidwa mpaka tsiku loyika maliro anga. Inu mudzakhala ndi osauka nthawi zonse, koma simudzakhala nane nthawi zonse.”
Pa nthawi imeneyi gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali kumeneko, ndipo linabwera, sichifukwa cha Iye yekha koma kudzaonanso Lazaro, amene anamuukitsa kwa akufa. Choncho akulu a ansembe anakonza njira yoti aphenso Lazaro, pakuti chifukwa cha iye Ayuda ambiri amapita kwa Yesu ndi kumukhulupirira.
Yesu Alowa mu Yerusalemu
Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu lomwe linabwera kuphwando linamva kuti Yesu anali mʼnjira kupita ku Yerusalemu. Iwo anatenga nthambi za kanjedza ndi kupita kukakumana naye, akufuwula kuti,
“Hosana!
“Wodala Iye amene akubwera mʼdzina la Ambuye!
“Yodala Mfumu ya Israeli!”
Yesu anapeza bulu wamngʼono ndi kukwerapo, monga kunalembedwa kuti:
“Usachite mantha mwana wamkazi wa Ziyoni;
taona mfumu yako ikubwera,
itakhala pa mwana wabulu.”
Poyamba ophunzira ake sanamvetsetse zonsezi. Koma pomwe Yesu analemekezedwa ndi pamene anazindikira kuti zinthu izi zinalembedwa ndipo kuti anamuchitira Iye.
Tsopano gulu la anthu lomwe linali naye pa nthawi imene amaukitsidwa Lazaro ku manda linapitiriza kuchitira umboni. Anthu ambiri, anapita kukakumana naye, chifukwa iwo anamva kuti Iye anachita chizindikiro chodabwitsachi. Choncho Afarisi anati kwa wina ndi mnzake, “Taonani, palibe chimene mwachitapo. Anthu onse akumutsatira Iye!”
Agriki Afuna Kuona Yesu
Tsopano panali Agriki ena pakati pa amene anapita kukapembedza ku phwando. Iwo anabwera kwa Filipo, wochokera ku Betisaida wa ku Galileya, ndi pempho, nati, “Akulu, ife tikufuna kuona Yesu.” Filipo anapita kukawuza Andreya; Andreya ndi Filipo pamodzi anakawuza Yesu.
Yesu anayankha kuti, “Nthawi yafika yakuti Mwana wa Munthu alemekezedwe. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti, ‘Mbewu ya tirigu imakhala imodzi yokha ngati sikugwa mʼnthaka ndi kufa. Koma ngati imfa, imabereka mbewu zambiri.’ Munthu amene amakonda moyo wake adzawutaya, pamene munthu amene amadana ndi moyo wake mʼdziko lino lapansi adzawusungira ku moyo wosatha. Aliyense amene atumikira Ine ayenera kunditsata; ndipo kumene Ine ndili, wotumikira wanga adzakhalanso komweko. Atate anga adzalemekeza amene atumikira Ine.
“Moyo wanga ukuvutika tsopano, kodi ndidzanena chiyani? Ndinene kuti Atate pulumutseni ku nthawi ino? Ayi. Chifukwa chimene Ine ndinabwera pa nthawi iyi ndi chimenechi. Atate, lemekezani dzina lanu!”
Kenaka mawu anabwera kuchokera kumwamba, “Ine ndalilemekeza, ndipo ndidzalilemekezanso.” Gulu la anthu lomwe linali pamenepo litamva linati, “Kwagunda bingu,” ena anati, “Mngelo wayankhula kwa Iye.”
Yesu anati, “Mawu awa abwera chifukwa cha inu osati chifukwa cha Ine. Ino tsopano ndi nthawi yachiweruzo pa dziko lapansi; tsopano olamulira wa dziko lapansi adzathamangitsidwa. Koma Ine, akadzandipachika pa dziko lapansi, ndidzakokera anthu onse kwa Ine.” Iye ananena izi kuti aonetse mmene adzafere.
Gulu la anthu linayankha kuti, “Ife tinamva kuchokera mʼmalamulo kuti Khristu adzakhala kwamuyaya, nanga bwanji Inu mukunena kuti, ‘Mwana wa Munthu ayenera kukwezedwa?’ Kodi Mwana wa Munthuyu ndani?”
Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Inu mukhala ndi kuwunika kwa nthawi pangʼono. Yendani pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mdima usakupitirireni. Munthu amene amayenda mu mdima sadziwa kumene akupita. Khulupirirani kuwunika, pamene mukanali ndi kuwunika, kuti mukhale ana a kuwunika.” Yesu atamaliza kuyankhula izi, Iye anachoka nabisala kuti asamuone.
Ayuda Apitirira Kusakhulupirira
Ngakhale Yesu anachita zizindikiro zodabwitsa zonsezi pamaso pawo, sanamukhulupirirebe. Izi zinakwaniritsa mawu a mneneri Yesaya kuti:
“Ambuye, wakhulupirira uthenga wathu ndani,
ndipo ndi kwa yani komwe mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa?”
Pa chifukwa cha ichi iwo sanakhulupirire, chifukwa Yesaya ananenanso kuti:
“Iye wachititsa khungu maso awo
ndi kuwumitsa mitima yawo,
kotero kuti iwo sangathe kuona ndi maso awo,
kapena kuzindikira ndi mitima yawo,
kapena kutembenuka kuti Ine ndikanawachiza.”
Yesaya ananena izi chifukwa anaona ulemerero wa Yesu ndi kuyankhula za Iye.
Komabe pa nthawi yomweyi ambiri ngakhale atsogoleri anakhulupirira Iye. Koma chifukwa cha Afarisi iwo sanavomereze chikhulupiriro chawo chifukwa amaopa kuti angawatulutse mʼsunagoge; pakuti iwo amakonda kuyamikiridwa ndi anthu kuposa kuyamikiridwa ndi Mulungu.
Kenaka Yesu anafuwula nati, “Munthu aliyense amene akhulupirira Ine, sakhulupirira Ine ndekha, komanso Iye amene anandituma Ine. Iye amene waona Ine, waonanso Iye amene anandituma Ine. Ine ndabwera mʼdziko lapansi monga kuwunika, kotero palibe amene amakhulupirira Ine nʼkumakhalabe mu mdima.
“Ndipo munthu amene amva mawu anga koma osawasunga, Ine sindimuweruza. Pakuti Ine sindinabwere kudzaweruza dziko lapansi, koma kudzapulumutsa. Iye amene akana Ine ndipo salandira mawu anga ali ndi womuweruza. Tsiku lomaliza mawu amene ndiyankhulawa adzamutsutsa. Pakuti Ine sindiyankhula mwa Ine ndekha, koma Atate amene anandituma amandilamulira choti ndinene ndi momwe ndinenere. Ine ndikudziwa kuti lamulo lake ndi moyo wosatha. Choncho chilichonse chimene Ine ndinena ndi chimene Atate andiwuza.”
Yesu Asambitsa Mapazi a Ophunzira Ake
Inali pafupifupi nthawi ya phwando la Paska. Yesu anadziwa kuti nthawi yafika yoti achoke mʼdziko lapansi ndi kupita kwa Atate. Atawakonda ake amene anali mʼdziko lapansi, Iye anawaonetsa chikondi chake chonse.
Atayamba kudya mgonero, mdierekezi anali atalowa kale mu mtima wa Yudasi Isikarioti mwana wa Simoni, kuti amupereke Yesu. Yesu podziwa kuti Atate anamupatsa Iye zonse mʼmanja mwake, ndi kuti Iye anachokera kwa Mulungu ndipo amabwerera kwa Mulunguyo; anayimirira kuchoka pa chakudya navula zovala zake natenga nsalu yopukutira nadzimanga mʼchiwuno mwake. Atachita izi, anathira madzi mʼbeseni ndi kuyamba kusambitsa mapazi a ophunzira ake, ndi kuwapukuta ndi chopukutira chimene anachimanga mʼchiwuno mwake.
Atafika pa Petro, Petroyo anati kwa Iye, “Ambuye, kodi mudzandisambitsa mapazi anga?”
Yesu anayankha kuti, “Iwe sukuzindikira tsopano chimene ndikuchita, koma udzazindikira mʼtsogolo.”
Petro anati, “Ayi, Inu simudzandisambitsa konse mapazi anga.”
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine sindisambitsa mapazi ako, ulibe gawo mwa Ine.”
Simoni Petro anayankha kuti, “Ambuye, osati mapazi okha komanso manja anga ndi mutu wanga womwe!”
Yesu anayankha kuti, “Munthu amene wasamba amangofunika kusamba mapazi ake okha chifukwa thupi lake lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, ngakhale kuti si aliyense mwa inu.” Pakuti Iye anadziwa amene adzamupereka, ndipo nʼchifukwa chake anati saliyense wa inu ali woyera.
Iye atamaliza kusambitsa mapazi awo anavala zovala zake ndi kubwerera pamalo pake. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mukuzindikira zimene ndakuchitirani inu? Inu mumanditcha Ine, ‘Mphunzitsi’ ndi ‘Mbuye,’ ndipo mumakhoza mukamatero, pakuti ichi ndi chimene Ine ndili. Tsono ngati Ine, Mbuye wanu ndi Mphunzitsi wanu, ndasambitsa mapazi anu, inunso muyenera kusambitsana mapazi anu. Ine ndakupatsani chitsanzo kuti muzichita monga Ine ndachitira. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti wantchito saposa mbuye wake, kapena wotumidwa kuposa amene wamutuma. Ngati inu mudziwa zinthu zimenezi, mudzakhala odala mukamazichita.
Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake
“Ine sindikunena za inu nonse. Ine ndikudziwa amene ndinawasankha. Koma izi zikukwaniritsa malemba: ‘Iye amene akudya nawo chakudya changa, ndiye amene anandiwukira.’
“Ine ndikukuwuzani tsopano zisanachitike zimenezi, kuti pamene zachitika, mudzakhulupirire kuti Ine Ndine. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene alandira amene Ine ndamutuma, alandiranso Ine. Aliyense amene alandira Ine, alandiranso amene anandituma.”
Yesu Aneneratu za Kuperekedwa Kwake
Yesu atanena izi, anavutika kwambiri mu mzimu ndipo anachitira umboni kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti mmodzi mwa inu adzandipereka.”
Ophunzira ake anapenyetsetsana wina ndi mnzake, posadziwa kuti amanena za yani. Mmodzi wa ophunzira ake amene Yesu anamukonda, anali atatsamira pachifuwa chake. Simoni Petro anamukodola wophunzirayo ndi kuti, “Mufunseni akunena za yani.”
Atamutsamiranso Yesuyo, anamufunsa Iye kuti, “Ambuye, kodi ndani?”
Yesu anayankha kuti, “Iye amene ndidzamupatsa buledi amene ndanyema ndikususa ndi ameneyo.” Kenaka, atasunsa gawo la buledi, Iye anapereka kwa Yudasi Isikarioti, mwana wa Simoni. Nthawi yomweyo Yudasi atangodya bulediyo, Satana analowa mwa Iye.
Yesu anamuwuza Iye kuti, “Chomwe ukufuna kuchita, chita msanga.” Koma panalibe ndi mmodzi yemwe pa chakudyapo amene anamvetsa chifukwa chimene Yesu ananenera izi kwa iye. Popeza Yudasi amasunga ndalama, ena amaganiza kuti Yesu amamuwuza iye kuti akagule zomwe zimafunika pa phwando, kapena kukapereka kanthu kena kake kwa osauka. Nthawi yomweyo Yudasi atangodya buledi, anatuluka, ndipo unali usiku.
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
Yudasi atatuluka, Yesu anati, “Tsopano Mwana wa Munthu walemekezedwa, ndipo mwa Iyeyu Mulungu walemekezedwanso. Ngati Mulungu walemekezedwa mwa Iye, Mulungu mwini adzalemekezanso Mwana, ndipo amulemekeza nthawi yomweyo.
“Ana anga, Ine ndikhala nanu kwa nthawi yochepa chabe. Inu mudzandifunafuna Ine, ndipo monga momwe ndinawawuzira Ayuda, choncho Ine ndikukuwuzani tsopano kuti, kumene Ine ndikupita, inu simungabwereko.
“Lamulo latsopano limene ndikukupatsani ndi lakuti: Kondanani wina ndi mnzake, monga momwe Ine ndinakonda inu. Nanunso mukondane wina ndi mnzake. Mukamakondana aliyense adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga.”
Simoni Petro anafunsa kuti, “Ambuye, kodi mukupita kuti?”
Yesu anayankha kuti, “Kumene Ine ndikupita iwe sunganditsatire tsopano, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”
Petro anafunsa kuti, “Ambuye, nʼchifukwa chiyani ine sindingakutsatireni tsopano? Ine ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha Inu.”
Kenaka Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe udzalolera kutaya moyo chifukwa cha Ine? Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti tambala asanalire, iwe udzandikana katatu!”
Yesu Atonthoza Ophunzira Ake
“Mtima wanu usavutike. Khulupirirani Mulungu; khulupirirani Inenso. Mʼnyumba mwa Atate anga muli zipinda zambiri. Kukanakhala kuti mulibemo ndikanakuwuzani. Ine ndikupita kumeneko kukakukonzerani malo. Ndipo ndikapita kukakukonzerani malo, ndidzabweranso kudzakutengani, kuti kumene kuli Ineko, inunso mukakhale komweko. Inu mukudziwa njira ya kumene Ine ndikupita.”
Yesu Njira ya kwa Atate
Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye ife sitikudziwa kumene Inu mukupita, nanga tingadziwe bwanji njirayo?”
Yesu anayankha kuti, “Ine ndine njira, choonadi ndi moyo. Palibe munthu angafike kwa Atate popanda kudzera mwa Ine. Mukanandidziwadi Ine, mukanadziwanso Atate anga. Kuyambira tsopano, mukuwadziwa ndipo mwawaona.”
Filipo anati, “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo ife tikhutitsidwa.”
Yesu anayankha kuti, “Kodi iwe Filipo, ndakhala pakati panu nthawi yonseyi ndipo iwe sukundidziwabe? Aliyense amene waona Ine, waonanso Atate. Tsono ukunena bwanji kuti, ‘Tionetseni Atate?’ Kodi sukukhulupirira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo Atate ali mwa Ine? Mawu amene Ine ndiyankhula kwa inu si mawu anga okha koma ndi mawu Atate wokhala mwa Ine, amene akugwira ntchito yake. Khulupirirani Ine pamene ndi kuti Ine ndili mwa Atate ndipo Atate ali mwa Ine. Koma ngati si chomwecho, khulupiriranitu Ine chifukwa cha ntchito zanga zodabwitsa. Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene akhulupirira Ine adzachita zimene Ine ndakhala ndikuchita. Iye adzachita ngakhale zinthu zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ndikupita kwa Atate. Ndipo Ine ndidzachita chilichonse chimene inu mudzapempha mʼdzina langa kuti Atate alemekezedwe mwa Mwana. Ngati mudzapempha kanthu kalikonse mʼdzina langa, Ine ndidzachita.
Lonjezo la Mzimu Woyera
“Ngati mundikonda Ine, sungani malamulo anga. Ine ndidzapempha Atate, ndipo adzakupatsani Nkhoswe ina kuti izikhala nanu nthawi zonse. Nkhosweyo ndiye Mzimu wachoonadi. Dziko lapansi silingalandire Nkhosweyi chifukwa samuona kapena kumudziwa. Koma inu mumamudziwa pakuti amakhala nanu ndipo adzakhala mwa inu. Ine sindikusiyani nokha kuti mukhale ana amasiye. Ine ndidzabweranso kwa inu. Patsala nthawi yochepa dziko lapansi silidzandionanso koma inu mudzandiona. Popeza kuti Ine ndili ndi moyo, inunso mudzakhala ndi moyo. Tsiku limenelo inu mudzazindikira kuti Ine ndili mwa Atate, ndipo inu muli mwa Ine, ndipo Ine ndili mwa inu. Iye amene amadziwa malamulo anga ndi kuwasunga ndiye amene amandikonda. Wokonda Ine adzakondedwa ndi Atate wanga ndipo Inenso ndidzamukonda ndikudzionetsa ndekha kwa iye.”
Kenaka Yudasi (osati Yudasi Isikarioti) anati, “Koma Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsa nokha kwa ife, osati ku dziko lapansi?”
Yesu anamuyankha kuti, “Ngati wina aliyense andikonda Ine, adzasunga mawu anga. Atate wanga adzamukonda, ndipo Ife tidzabwera ndi kukhala naye. Iye amene sandikonda Ine sasunga mawu anga. Mawu awa amene mukumva si anga ndi a Atate amene anandituma Ine.
“Ndayankhula zonsezi ndikanali nanu. Koma Nkhosweyo, Mzimu Woyera, amene Atate adzamutumiza mʼdzina langa adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndipo adzakukumbutsani zonse zimene ndinakuwuzani. Ine ndikukusiyirani mtendere. Ndikukupatsani mtendere wanga. Ine sindikukupatsani monga dziko lapansi limaperekera. Mtima wanu usavutike ndipo musachite mantha.
“Inu munamva Ine ndikunena kuti, ‘Ine ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Mukanandikonda, mukanasangalala kuti Ine ndikupita kwa Atate, pakuti Atate ndi wamkulu kuposa Ine. Ine ndakuwuzani tsopano zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire. Ine sindiyankhulanso nanu zambiri nthawi yayitali popeza wolamulira dziko lapansi akubwera. Iye alibe mphamvu pa Ine, koma kuti dziko lapansi lizindikire kuti Ine ndimakonda Atate ndi kuti ndimachita zokhazokha zimene Atate wandilamulira Ine.
“Nyamukani; tizipita.”
Mpesa ndi Nthambi
“Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
“Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.
“Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’
Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu
“Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’
Ntchito ya Mzimu Woyera
“Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”
“Ine ndakuwuzani zonsezi kuti musadzakhumudwe. Iwo adzakuchotsani mʼsunagoge mwawo. Kunena zoona, nthawi ikubwera imene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti akutumikira Mulungu. Iwo adzachita zoterozo chifukwa sanadziwe Atate kapena Inenso. Ine ndakuwuzani izi kuti nthawi ikadzafika mudzakumbukire kuti Ine ndinakuchenjezani kale. Ine sindinakuwuzeni izi poyamba paja chifukwa ndinali nanu.”
Ntchito ya Mzimu Woyera
“Tsopano Ine ndikupita kwa Iye amene anandituma koma palibe wina mwa inu akundifunsa kuti, ‘Kodi mukupita kuti?’ Muli ndi chisoni kwambiri chifukwa ndakuwuzani zimene. Komatu ndakuwuzani zoona. Ine ndikuti kuli bwino kwa inu kuti ndichoke. Ngati sindichoka, Nkhosweyo sidzabwera kwa inu, koma ngati Ine ndipita, ndidzamutumiza kwa inu. Iye akabwera, adzatsutsa dziko lapansi za uchimo, zachilungamo ndi zachiweruzo. Za uchimo, chifukwa anthu sakhulupirira Ine. Za chilungamo, chifukwa Ine ndi kupita kwa Atate, kumene simudzandionanso. Za chiweruzo, chifukwa wolamulira dziko lino lapansi waweruzidwa tsopano.
“Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani. Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”
Chisoni cha Ophunzira Chisandulika Chimwemwe
Yesu anapitiriza kuyankhula kuti, “Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso, ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso.”
Ena a ophunzira ake anati kwa wina ndi mnzake, “Kodi Iye akutanthauza chiyani ponena kuti, ‘Mwa kanthawi kochepa, simudzandionanso,’ ndi ‘ndipo patatha nthawi pangʼono mudzandionanso,’ ndiponso ‘chifukwa ndikupita kwa Atate?’ ” Iwo anapitiriza kufunsana kuti, “Kodi akutanthauza chiyani, ‘kanthawi kochepa?’ Ife sitikumvetsetsa chimene Iye akuyankhula.”
Yesu anadziwa kuti ankafuna kuti amufunse za zimenezi, choncho anawafunsa kuti, “Kodi mukufunsana wina ndi mnzake chimene Ine ndimatanthauza pamene ndinati, ‘Mwa kanthawi kochepa simudzandionanso,’ ndi ‘patatha nthawi pangʼono mudzandionanso?’ Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti inu mudzalira ndi kubuma pomwe dziko lapansi lidzakhale likukondwera. Inu mudzamva chisoni, koma chisoni chanu chidzasandulika chimwemwe. Mayi akamabereka mwana amamva ululu chifukwa nthawi yake yafika; koma mwana wake akabadwa amayiwala ululu wake chifukwa cha chimwemwe chake chakuti mwana wabadwa mʼdziko lapansi. Chimodzimodzinso ndi inu. Tsopano ino ndi nthawi yanu yomva chisoni, koma Ine ndidzakuonaninso ndipo inu mudzasangalala, ndipo palibe amene adzachotsa chimwemwe chanu. Tsiku limenelo inu simudzandipemphanso kalikonse. Ine ndikukuwuzani zoona kuti Atate anga adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. Mpaka tsopano simunapemphe kalikonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.
“Ngakhale ndakhala ndikuyankhula mʼmafanizo, nthawi ikubwera imene Ine sindidzagwiritsanso ntchito mafanizo otere koma ndidzakuwuzani momveka za Atate anga. Tsiku limenelo inu mudzapempha mʼdzina langa. Ine sindikunena kuti ndidzapempha Atate mʼmalo mwanu ayi. Atate mwini anakukondani chifukwa inu mwandikonda Ine ndipo mwakhulupirira kuti Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate. Ine ndinabwera kuchokera kwa Atate ndi kulowa mʼdziko lapansi. Tsopano ndikulisiya dziko lapansi kubwerera kwa Atate.”
Kenaka ophunzira ake anati, “Tsopano mukuyankhula momveka bwino ndi mopanda mafanizo. Tsopano ife tikuona kuti Inu mumadziwa zinthu zonse ndi kuti sipafunika wina aliyense kukufunsani. Mwa ichi ife takhulupirira kuti Inu munachokera kwa Mulungu.”
Yesu anawafunsa kuti, “Kodi tsopano mwakhulupirira?” Koma nthawi ikubwera ndipo yafika, pamene inu mudzabalalitsidwa, aliyense ku nyumba yake. Inu mudzandisiya ndekhandekha. Koma Ine sindili ndekha, pakuti Atate anga ali nane.
“Ine ndakuwuzani izi kuti mwa Ine mukhale nawo mtendere. Mʼdziko lapansi mudzakhala nawo mavuto. Koma limbikani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko lapansi.”
Yesu Adzipempherera Yekha
Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera:
“Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe.
Yesu Apempherera Ophunzira Ake
“Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.
“Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.
Yesu Apempherera Okhulupirira Onse
“Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.
“Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.
“Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”
Amugwira Yesu
Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo.
Tsopano Yudasi, amene anamupereka amadziwa malowo chifukwa Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. Choncho Yudasi anabwera ku munda, akutsogolera gulu la asilikali ndi akuluakulu ena ochokera kwa akulu a ansembe ndi Afarisi. Iwo anali atanyamula miyuni, nyale ndi zida.
Yesu, podziwa zonse zimene zimati zichitike kwa Iye, anatuluka ndi kuwafunsa kuti, “Kodi mukufuna ndani?”
Iwo anayankha kuti, “Yesu wa ku Nazareti.”
Yesu anati, “Ndine.” (Ndipo Yudasi womuperekayo anali atayima nawo pamenepo). Pamene Yesu anati, “Ndine,” iwo anabwerera mʼmbuyo ndi kugwa pansi.
Iye anawafunsanso kuti, “Kodi mukumufuna ndani?”
Ndipo iwo anati, “Yesu wa ku Nazareti.”
Yesu anayankha kuti, “Ine ndakuwuzani kuti Ndine. Ngati inu mukufuna Ine, asiyeni anthu awa apite.” Izi zinachitika kuti mawu amene Iye anayankhula akwaniritsidwe: “Ine sindinataye ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene mwandipatsa.”
Kenaka Simoni amene anali ndi lupanga analitulutsa ndi kutema nalo wantchito wa wamkulu wa ansembe, nadula khutu lake la kudzanja lamanja. (Dzina la wantchitoyo ndi Makusi).
Yesu analamula Petro kuti, “Bwezera lupanga mʼchimake! Kodi Ine ndisamwere chikho chimene Atate andipatsa?”
Amutengera Yesu kwa Anasi
Kenaka gulu la asilikali ndi olamulira wawo ndi akuluakulu a Ayuda anamugwira Yesu. Iwo anamumanga. Poyamba anapita naye kwa Anasi amene anali mkamwini wa Kayafa, mkulu wa ansembe chaka chimenecho. Kayafa anali amene analangiza Ayuda kuti kukanakhala kwabwino ngati munthu mmodzi akanafera anthu.
Petro Akana Yesu Koyamba
Simoni Petro ndi ophunzira wina ankamutsatira Yesu chifukwa ophunzira uyu amadziwika kwa mkulu wa ansembe. Iye analowa ndi Yesu mʼbwalo la mkulu wa ansembe koma Petro anadikira kunja pa khomo. Ophunzira winayo amene amadziwika kwa mkulu wa ansembe, anatuluka ndi kuyankhula ndi mtsikana amene anali mlonda wa pa khomo ndi kumulowetsa Petro.
Mtsikanayo anafunsa Petro kuti, “Kodi iwe sindiwe mmodzi wa ophunzira a Munthu uyu?”
Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
Popeza kunkazizira, anyamata antchito ndi akuluakulu ena anasonkha moto wamakala namawotha atayimirira mozungulira. Petro nayenso anayimirira pamodzi ndi iwo namawotha nawo motowo.
Mkulu wa Ansembe Amufunsa Yesu
Pa nthawi imeneyi, mkulu wa ansembe anamufunsa Yesu za ophunzira ake ndi chiphunzitso chake.
Yesu anayankha kuti, “Ine ndinayankhula poyera ku dziko lapansi. Nthawi zonse ndimaphunzitsa mʼsunagoge kapena mʼNyumba ya Mulungu kumene Ayuda onse amasonkhana pamodzi. Ine sindimanena kanthu mseri. Nʼchifukwa chiyani mukundifunsa Ine? Afunseni amene amamva. Zoonadi akudziwa zimene Ine ndinanena.”
Yesu atanena izi, mmodzi wa akuluakulu amene anali pafupi anamumenya kumaso. Iye anafunsa kuti, “Mayankhidwe awa ndi woti ndi kuyankha mkulu wa ansembe?”
Yesu anayankha kuti, “Ngati Ine ndanena kanthu kolakwika, chitirani umboni chimene ndalakwa. Koma ngati ndanena zoona, nʼchifukwa chiyani mwandimenya?” Kenaka Anasi anamutumiza Iye, ali womangidwabe, kwa Kayafa, mkulu wa ansembe.
Petro Akana Yesu Kachiwiri ndi Kachitatu
Pamene Simoni Petro anali chiyimirire kuwotha moto, anafunsidwa kuti, “Kodi iwe si mmodzi wa ophunzira ake?”
Iye anayankha kuti, “Ayi, sindine.”
Mmodzi wa antchito a mkulu wa ansembe, mʼbale wa munthu amene anadulidwa khutu ndi Petro anamutsutsa iye kuti, “Kodi sindinakuone iwe pamodzi ndi Iye mʼmunda muja?” Petro anakananso, ndipo pa nthawi yomweyo tambala analira.
Yesu ku Bwalo la Pilato
Kenaka Ayuda anamutenga Yesu kuchoka kwa Kayafa ndi kupita ku nyumba yaufumu ya bwanamkubwa wa Chiroma. Tsopano kunali mmamawa, ndipo polewa kudetsedwa monga mwa mwambo Ayuda sanalowe mʼnyumba yaufumuyo; iwo anafuna kuti adye Paska. Choncho Pilato anatuluka napita kwa iwo ndipo anati, “Kodi ndi milandu yanji imene mukumuzenga munthu uyu?”
Iwo anayankha kuti, “Ngati Iye akanakhala kuti si wolakwa, ife sitikanamupereka kwa inu.”
Pilato anati, “Mutengeni inu eni ake ndi kumuweruza Iye monga mwa malamulo anu.”
Ayuda anatsutsa nati, “Koma tilibe ulamuliro wakupha aliyense.” Izi zinachitika kuti mawu a Yesu amene anayankhula kusonyeza mtundu wa imfa imene Iye anati adzafe nayo akwaniritsidwe.
Kenaka Pilato anapita mʼkati mwa nyumba yaufumu nayitanitsa Yesu, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi iwe ndi mfumu ya Ayuda?”
Yesu anafunsa kuti, “Kodi amenewo ndi maganizo anu wokha? Kapena kuti ena anakuwuzani za Ine?”
Pilato anayankha kuti, “Kodi iwe ukuganiza kuti ine ndine Myuda? Ndi anthu ako ndi akulu a ansembe ako amene akupereka iwe kwa ine. Kodi walakwanji?”
Yesu anati, “Ufumu wanga si wa dziko lapansi lino. Ukanakhala wa pansi pano, antchito anga akanachita nkhondo kulepheretsa Ayuda kundigwira. Koma tsopano ufumu wanga ndi wochokera kumalo ena.”
Pilato anati, “Kani ndiwe mfumu!”
Yesu anayankha kuti, “Inu mwalondola ponena kuti, Ine ndine mfumu. Kunena zoona, Ine ndinabadwa chifukwa cha chimenechi, ndipo nʼchifukwa chake ndinabwera mʼdziko lapansi, kudzachitira umboni choonadi. Aliyense amene ali mbali yachoonadi amamvera mawu anga.”
Pilato anafunsa kuti, “Kodi choonadi nʼchiyani?” Ndi mawu awa iye anapitanso kwa Ayuda ndipo anati, “Ine sindikupeza mlandu mwa Iye. Koma ndi mwambo wanu kuti pa nthawi ya Paska, ine ndikumasulireni wamʼndende mmodzi. Kodi mufuna ndikumasulireni ‘Mfumu ya Ayuda?’ ”
Iwo anafuwula nati, “Ameneyu ayi! Mutipatse ife Baraba!” Barabayo anali wachifwamba.
Yesu Aweruzidwa kuti Aphedwe
Kenaka Pilato anatenga Yesu namukwapula mwankhanza. Asilikali analuka nkhata yaminga ndi kumuveka pamutu pake. Kenaka anamuveka mkanjo wapepo ndipo ankapita kwa Iye mobwerezabwereza ndi kumanena kuti, “Moni mfumu ya Ayuda?” Ndipo amamumenya makofi.
Pilato anatulukanso ndipo anati kwa Ayuda, “Taonani, ine ndikumubweretsa kuti inu mudziwe kuti ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.” Pamenepo Yesu anatuluka atavala nkhata yaminga ndi mkanjo wapepo ndipo Pilato anawawuza kuti, “Nayu munthu uja!”
Atangomuona Iye akulu a ansembe ndi akuluakulu ena anafuwula kuti, “Mpachikeni! Mpachikeni!”
Koma Pilato anayankha kuti, “Inu mutengeni ndi kumupachika. Koma ine sindikupeza chifukwa chomuyimbira mlandu.”
Ayuda anayimirira nati, “Ife tili ndi lamulo, ndipo molingana ndi lamulolo, Iyeyu ayenera kuphedwa chifukwa akudzitcha kuti ndi Mwana wa Mulungu.”
Pilato atamva zimenezi, anachita mantha kwambiri, ndipo anabwereranso mʼnyumba yaufumu. Iye anafunsa Yesu kuti, “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanayankhe. Pilato anati, “Kodi ukukana kundiyankhula ine? Kodi sukuzindikira kuti ine ndili ndi mphamvu yokumasula ndiponso mphamvu yokupachika?”
Yesu anayankha kuti, “Inu simukanakhala ndi mphamvu pa Ine akanapanda kukupatsani kumwamba. Nʼchifukwa chake amene wandipereka Ine kwa inu ndiye wochimwa kwambiri.”
Kuyambira pamenepo Pilato anayesa kuti amumasule Yesu, koma Ayuda anapitirira kufuwula kuti, “Ngati mumumasula munthuyu kuti apite, inu si bwenzi la Kaisara.”
Pilato atamva zimenezi, iye anamutulutsa Yesu kunja ndi kukhala pansi pa mpando wa woweruza pamalo otchedwa Mwala Wowaka (umene pa Chiaramaiki ndi Gabata). Linali tsiku lokonzekera Sabata la Paska ndipo nthawi inali ora lachisanu ndi chimodzi masana.
Pilato anati kwa Ayuda, “Nayi mfumu yanu.”
Koma iwo anafuwula kuti, “Choka nayeni! Choka nayeni! Mpachikeni!”
Pilato anafunsa kuti, “Kodi ine ndipachike mfumu yanuyi?”
Akulu a ansembe anayankha kuti, “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.”
Pomaliza Pilato anamupereka kwa iwo kuti akapachikidwe. Choncho asilikali anamutenga Yesu.
Kupachikidwa kwa Yesu
Atanyamula mtanda wake, anapita kumalo otchedwa “Malo a Bade” (mʼChiaramaiki amatchedwa Gologota). Pamenepo iwo anamupachika Iye pamodzi ndi anthu ena awiri, mmodzi mbali ina ndi wina mbali inanso ndipo Yesu pakati.
Pilato analemba chikwangwani chomwe anachikhoma pa mtandapo. Panalembedwa mawu akuti, yesu wa ku nazareti, mfumu ya ayuda. Ayuda ambiri anawerenga chikwangwanichi, pakuti pamalo pamene Yesu anapachikidwapo panali pafupi ndi mzinda ndipo chikwangwanicho chinalembedwa mu Chiaramaiki, Chilatini ndi Chigriki. Kenaka mkulu wa ansembe wa Ayuda anakadandaula kwa Pilato nati, “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti munthuyu amadzitcha kuti ndi mfumu ya Ayuda.”
Pilato anayankha kuti, “Chimene ine ndalemba, ndalemba.”
Asilikali atamupachika Yesu, anatenga zovala zake ndi kuzigawa zigawo zinayi, gawo limodzi la aliyense wa iwo, ndi kutsala mwinjiro wamʼkati wokha. Chovala ichi chinawombedwa kuyambira pamwamba mpaka pansi wopanda msoko.
Iwo anati kwa wina ndi mnzake, “Tiyeni tisachingʼambe koma tichite maere kuti tione amene achitenge.”
Izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe amene anati,
“Iwo anagawana zovala zanga pakati pawo
ndi kuchita maere pa zovala zangazo.”
Choncho izi ndi zimene asilikali anachita.
Pafupi ndi mtanda wa Yesu panayima amayi ake, mngʼono wa amayi ake, Mariya mkazi wa Kaliyopa ndi Mariya wa ku Magadala. Yesu ataona amayi ake pamenepo ndi wophunzira amene Iye anamukonda atayima pafupipo, Iye anati kwa amayi ake, “Amayi nayu mwana wanu.” Anawuzanso wophunzirayo kuti, “Nawa amayi ako.” Kuyambira nthawi imeneyo, wophunzirayo anatenga amayiwo kupita nawo kwawo.
Imfa ya Yesu
Atadziwa kuti zonse zatha tsopano komanso kuti malemba akwaniritsidwe, Yesu anati, “Ine ndili ndi ludzu.” Pomwepo panali mtsuko wodzaza ndi vinyo wosasa, choncho iwo ananyika chinkhupule ndi kuchisomeka ku mtengo wa hisope nachifikitsa kukamwa kwa Yesu. Yesu atalandira chakumwachi anati, “Kwatha.” Ndipo Iye anaweramitsa mutu wake napereka mzimu wake.
Popeza linali Tsiku Lokonzekera ndipo tsiku linalo linali Sabata lapadera; Ayuda sanafune kuti mitembo ikhale pa mtanda pa Sabata, iwo anapempha Pilato kuti akathyole miyendo ndi kutsitsa mitemboyo. Chifukwa chake asilikali anabwera ndi kuthyola miyendo ya munthu oyamba amene anapachikidwa ndi Yesu ndipo kenaka ya winayo. Koma atafika pa Yesu ndi kupeza kuti anali atamwalira kale, iwo sanathyole miyendo yake. Mʼmalo mwake, mmodzi wa asilikaliwo anamubaya Yesu ndi mkondo mʼnthiti, ndipo nthawi yomweyo munatuluka magazi ndi madzi. Munthu amene anaona izi wapereka umboni ndipo umboni wake ndi woona. Iye akudziwa kuti akunena choonadi kuti inunso mukhulupirire. Zinthu izi zinachitika kuti malemba akwaniritsidwe: “Palibe limodzi la mafupa limene lidzathyoledwa,” ndi monga lemba linanso linena, “Iwo adzayangʼana Iye amene iwo anamubaya.”
Yesu Ayikidwa Mʼmanda
Kenaka, Yosefe wa ku Arimateyu anakapempha mtembo wa Yesu kwa Pilato. Tsono Yosefe anali wophunzira wa Yesu koma mobisa chifukwa iye ankaopa Ayuda. Atalandira chilolezo kwa Pilato, anakatsitsa mtembo wa Yesu. Nekodimo, munthu amene poyamba pake anabwera kwa Yesu usiku, anatenga mafuta osakaniza ndi mure ndi aloe wolemera pafupifupi makilogalamu 32. Pamenepo anatenga mtembo wa Yesu nawukulunga pamodzi ndi zonunkhiritsa mu nsalu za mtundu woyera monga mwa mwambo wa maliro wa Ayuda. Pamalo pamene anapachikidwa Yesu panali munda ndipo mʼmundamo munali manda atsopano mʼmene munali simunayikidwemo aliyense. Chifukwa linali Tsiku la Ayuda Lokonzekera ndi kuti mandawo anali pafupipo, iwo anayika Yesu mʼmenemo.
Yesu Auka kwa Akufa
Mmamawa tsiku loyamba la sabata, kukanali kamdimabe, Mariya wa ku Magadala anapita ku manda ndipo anaona kuti mwala unali utachotsedwa pa khomo la manda. Choncho anabwerera akuthamanga kwa Simoni Petro ndi wophunzira winayo, amene Yesu anamukonda, ndipo anati, “Iwo amuchotsa Ambuye mʼmanda, ndipo ife sitikudziwa kumene iwo amuyika Iye!”
Choncho Petro ndi wophunzira winayo ananyamuka kupita ku manda. Onse awiri anathamanga pamodzi koma wophunzira winayo anamupitirira Petro, nafika ku manda moyambirira. Ndipo mmene anawerama nasuzumira mʼkati mwa manda anaona nsalu zili potero koma sanalowemo. Kenaka Simoni Petro, amene anali pambuyo pake, anafika ndi kulowa mʼmanda. Iye anaona nsaluzo zili pamenepo, pamodzinso ndi nsalu imene anakulungira nayo mutu wa Yesu. Nsaluyi inali yopindidwa pa yokha yosiyanitsidwa ndi inayo. Pomaliza wophunzira winayo, amene anafika ku manda moyambirira, analowanso mʼkati, iye anaona ndi kukhulupirira. (Iwo sanazindikire kuchokera mʼmalemba kuti Yesu anayanera kuuka kuchokera kwa akufa).
Yesu Aonekera kwa Mariya wa ku Magadala
Kenaka ophunzira anabwerera ku nyumba zawo, koma Mariya anayima kunja kwa manda akulira. Pamene akulira, anawerama ndi kusuzumira mʼmanda ndipo anaona angelo awiri atavala zoyera, atakhala pamene panali mtembo wa Yesu, mmodzi kumutu ndi wina kumapazi.
Iwo anamufunsa iye kuti, “Amayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?”
Iye anati, “Amuchotsa Mbuye wanga, ndipo ine sindikudziwa kumene iwo amuyika.” Atanena izi, iye anatembenuka ndipo anaona Yesu atayima potero koma iye sanazindikire kuti anali Yesu.
Iye anati, “Amayi, mukulira chifukwa chiyani? Ndani amene mukumufunafuna?”
Poganiza kuti anali mwini munda, iye anati, “Bwana, ngati inu mwamuchotsa, ndiwuzeni kumene mwamuyika, ndipo ine ndikamutenga.”
Yesu anati kwa iye, “Mariya.”
Anatembenukira kwa Iye nafuwula mu Chiaramaiki kuti, “Raboni!” (kutanthauza Mphunzitsi).
Yesu anati, “Usandigwire Ine, pakuti sindinapite kwa Atate. Mʼmalo mwake pita kwa abale anga ndikukawawuza kuti, ndikupita kwa Atate ndi kwa Atate anunso, kwa Mulungu wanga ndi Mulungu wanunso.”
Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzira ndi uthenga wakuti, “Ndamuona Ambuye!” Iye anawawuza iwo kuti Yesu ananena zinthu izi kwa iye.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira ake Tomasi Palibe
Madzulo a tsiku limenelo limene linali loyamba la Sabata ophunzira ake ali pamodzi, atatseka ndi kukhoma zitseko chifukwa choopa Ayuda, Yesu anabwera ndi kuyima pakati pawo nati, “Mtendere ukhale nanu!” Iye atatha kunena izi, anawaonetsa manja ake ndi mʼnthiti mwake. Ophunzira anasangalala kwambiri pamene anaona Ambuye.
Yesu anatinso, “Mtendere ukhale nanu! Monga Atate anandituma Ine, Inenso ndikukutumani.” Ndi mawu amenewo Iye anawapumira ndipo anati, “Landirani Mzimu Woyera. Ngati mukhululukira aliyense machimo ake, iwo akhululukidwa; ngati simuwakhululukira, iwo sanakhululukidwe.”
Yesu Aonekera kwa Tomasi
Koma Tomasi (otchedwa Didimo), mmodzi wa khumi ndi awiriwo, sanali ndi ophunzira pamene Yesu anabwera. Ophunzira enawo atamuwuza Tomasi kuti iwo anaona Ambuye, iye ananenetsa kuti, “Pokhapokha nditaona zizindikiro za misomali mʼmanja ake ndi kuyikamo chala changa mʼmene munali misomali ndi kukhudza dzanja langa mʼnthiti mwake, ine sindidzakhulupirira.”
Patapita sabata, ophunzira ake analinso mʼnyumbamo ndipo Tomasi anali nawo. Ngakhale makomo anali otsekedwa, Yesu anabwera nayima pakati pawo, ndipo anati, “Mtendere ukhale nanu!” Kenaka anati kwa Tomasi, “Ika chala chako apa; ona manja anga. Tambasula dzanja lako ndi kukhudza mʼnthiti mwanga. Leka kukayika, khulupirira.”
Tomasi anati kwa Iye, “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!”
Kenaka Yesu anamuwuza kuti, “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona Ine? Ndi odala amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”
Cholinga cha Uthenga Wabwino wa Yohane
Yesu anachita zodabwitsa zambiri pamaso pa ophunzira ake zimene sizinalembedwe mʼbuku lino. Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndi kuti mukakhulupirira mukhale nawo moyo mʼdzina lake.
Yesu Aonekera kwa Ophunzira ku Nyanja ya Tiberiya
Zitatha izi Yesu anaonekeranso kwa ophunzira ake, mʼmbali mwa nyanja ya Tiberiya. Anadzionetsera motere: Simoni Petro, Tomasi (otchedwa Didimo), Natanieli wochokera ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzira ena awiri anali limodzi. Simoni Petro anawawuza iwo kuti, “Ine ndikupita kukasodza,” ndipo iwo anati, “ife tipita nawe.” Choncho anapita ndi kulowa mʼbwato, koma usiku umenewo sanagwire kanthu.
Mmamawa, Yesu anayimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzira ake sanazindikire kuti anali Yesu.
Yesu anawafunsa iwo kuti, “Anzanga, kodi muli nsomba?”
Iwo anayankha kuti, “Ayi.”
Iye anati, “Ponyani khoka lanu kudzanja lamanja la bwato lanu ndipo mupha kanthu.” Atatero, iwo analephera kukoka ukonde chifukwa chakuchuluka kwa nsomba.
Kenaka ophunzira amene Yesu amamukonda anati kwa Petro, “Ndi Ambuye!” Petro atangomva iye akunena kuti ndi Ambuye, iye anavala chovala chake (pakuti anali atavula) ndipo analumphira mʼnyanja. Ophunzira enawo analowa mʼbwato akukoka ukonde odzaza ndi nsomba, popeza iwo sanali kutali kuchokera ku mtunda, pafupifupi mamita makumi asanu ndi anayi. Atafika pa mtunda, iwo anaona moto wamakala pamenepo ndi nsomba, ndi buledi.
Yesu anawawuza kuti, “Tabweretsa nsomba zina mwagwirazo.”
Simoni Petro anakwera mʼbwato ndi kukokera khoka ku gombe, lodzaza ndi nsomba zikuluzikulu 153, komabe ndi nsomba zochuluka chotero khoka silinangʼambike. Yesu anawawuza kuti, “Bwerani mudzalandire chakudya chammawa.” Palibe mmodzi wa ophunzira anayesa kumufunsa Iye, “Kodi ndinu ndani?” Iwo anadziwa kuti anali Ambuye. Yesu anabwera, natenga buledi ndikuwapatsa iwo, ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsomba. Aka kanali tsopano kachitatu Yesu akuonekera kwa ophunzira ake Iye ataukitsidwa kwa akufa.
Yesu Abwezeretsa Petro
Iwo atamaliza kudya chakudya chammawa, Yesu anati kwa Simoni Petro, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikonda Ine kuposa mmene amandikondera awa?”
Iye anati, “Inde Ambuye, Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Samala ana ankhosa anga.”
Yesu anatinso, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”
Iye anayankha kuti, “Inde, Ambuye, Inu mukudziwa kuti ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Weta nkhosa zanga.”
Yesu anati kwa iye kachitatu, “Simoni, mwana wa Yohane, kodi umandikondadi Ine?”
Petro anadzimvera chisoni chifukwa Yesu anamufunsa kachitatu kuti, “Kodi umandikonda Ine?” Iye anati, “Ambuye, Inu mudziwa zinthu zonse. Inu mukudziwa kuti Ine ndimakukondani.”
Yesu anati, “Dyetsa nkhosa zanga. Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti uli wamngʼono unkadziveka wekha lamba ndi kupita kumene unkafuna; koma ukadzakalamba udzatambasula manja ako ndipo wina wake adzakuveka ndikukutsogolera kupita kumene sukufuna kupita.” Yesu ananena izi kumuzindikiritsa mtundu wa imfa imene Petro adzalemekezera nayo Mulungu. Kenaka Iye anati kwa Petro, “Nditsate Ine!”
Petro anatembenuka ndi kuona kuti ophunzira amene Yesu amamukonda amawatsatira iwo. (Uyu ndi amene anatsamira pachifuwa cha Yesu pa chakudya chamadzulo ndipo iye anati, “Ambuye, kodi ndi ndani amene adzakuperekani Inu?” Petro atamuona iye, anafunsa kuti, “Ambuye, nanga uyu?”
Yesu anayankha kuti, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo? Iwe uyenera kunditsata Ine.” Chifukwa cha ichi mbiri inafala pakati pa abale kuti wophunzira uyu sadzafa. Koma Yesu sananene kuti iye sadzafa. Iye anati, “Ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka nditabweranso, zikukukhudza bwanji zimenezo?”
Uyu ndi wophunzira amene akuchitira umboni ndipo ndi amene analemba. Ife tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
Koma palinso zina zambiri zimene Yesu anachita. Zikanalembedwa zonsezi, ndikhulupirira dziko lonse lapansi likanasowa malo osungirako mabuku onse amene akanalembedwa.