- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
YEREMIYA
Yeremiya
Yeremiya
Yer
Yeremiya
Mawu a Yeremiya mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, mʼdziko la Benjamini. Mawuwa Yehova anayankhula naye mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya Yuda. Yehova anayankhulanso naye pa nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu anapita ku ukapolo.
Kuyitanidwa kwa Yeremiya
Yehova anayankhula nane kuti,
“Ndisanakuwumbe mʼmimba mwa amayi ako ndinali nditakudziwa kale,
iwe usanabadwe ndinali nditakupatula kale;
ndinakuyika kuti ukhale mneneri kwa anthu a mitundu yonse.”
Ine ndinati, “Haa! Ambuye Yehova, ine sinditha kuyankhula; popeza ndikanali wamngʼono.”
Koma Yehova anandiwuza kuti, “Usanene kuti, ‘Ndikanali wamngʼono’ popeza udzapita kwa munthu aliyense kumene ndidzakutuma ndi kunena chilichonse chimene ndidzakulamulira. Usawaope, pakuti Ine ndili nawe, ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
Pamenepo Yehova anatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga, nandiwuza kuti, “Taona, tsopano ndayika mawu anga mʼkamwa mwako. Lero ndakusankha kuti ukhale ndi ulamuliro pa mitundu ya anthu ndi pa maufumu awo kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kugumula, kuti uwamange ndi kudzala.”
Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona nthambi ya mtengo wa mtowo.”
Yehova anandiwuza kuti, “Waona bwino, chifukwa Ine ndikuonetsetsa kuti mawu angawa akwaniritsidwe.”
Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti, “Kodi ukuona chiyani?”
Ine ndinayankha kuti, “Ndikuona mʼphika wa madzi owira, ndipo wagudukira kuno kummwera.”
Yehova anandiwuza kuti, “Mavuto a anthu onse okhala mʼdziko lino adzachokera kumpoto. Ine ndikuyitana anthu onse a ku maufumu a kumpoto,” akutero Yehova.
“Mafumu awo adzabwera ndipo aliyense adzakhazika mpando wake waufumu
polowera pa zipata za Yerusalemu;
iwo adzabwera ndi kuzungulira makoma ake
ndiponso midzi yonse ya dziko la Yuda.
Ndidzatulutsa mlandu wanga ndi iwo
chifukwa cha zoyipa zimene anachita pondisiya Ine.
Iwo anakafukiza lubani kwa milungu ina,
ndi kupembedza zimene anapanga ndi manja awo.
“Koma iwe Yeremiya konzeka! Nyamuka ndipo ukawawuze zonse zimene ndakulamulira. Usachite nawo mantha, kuopa kuti Ine ndingakuchititse mantha iwo akuona. Taona, lero ndakupanga kukhala ngati mzinda wotetezedwa, ngati mzati wachitsulo ndiponso ngati makoma a mkuwa kuti usaopsedwe ndi munthu aliyense wa mʼdzikomo; kaya ndi mafumu a Yuda, akuluakulu ake, ansembe ake, kapena munthu wamba wa mʼdzikomo. Iwo adzalimbana nawe koma sadzakugonjetsa, popeza Ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akutero Yehova.
Aisraeli Asiya Mulungu
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti Yehova akuti,
“ ‘Ine ndikukumbukira mmene umakhulupirikira pa unyamata wako,
mmene unkandikondera ngati momwe amachitira mkwatibwi,
mmene unkanditsata mʼchipululu muja;
mʼdziko losadzalamo kanthu.
Israeli anali wopatulika wa Yehova,
anali ngati zipatso zake zoyamba kucha pa nthawi yokolola;
onse amene anamuzunza anapezeka kuti ndi olakwa
ndipo mavuto anawagwera,’ ”
akutero Yehova.
Imvani mawu a Yehova, inu zidzukulu za Yakobo,
inu mafuko onse a Israeli.
Yehova akuti,
“Kodi makolo anu anandipeza nʼcholakwa chanji,
kuti andithawe?
Iwo anatsata milungu yachabechabe,
nawonso nʼkusanduka achabechabe.
Iwo sanafunse nʼkomwe kuti, ‘Kodi Yehova ali kuti,
amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto
natitsogolera mʼchipululu mʼdziko lowuma
ndi lokumbikakumbika,
mʼdziko lopanda mvula ndi la mdima,
dziko limene munthu sadutsamo ndipo simukhala munthu aliyense?’
Ndinakufikitsani ku dziko lachonde
kuti mudye zipatso zake ndi zabwino zake zina.
Koma inu mutafika munaliyipitsa dziko langa
ndi kusandutsa cholowa changa kukhala chonyansa.
Ansembe nawonso sanafunse kuti,
‘Yehova ali kuti?’
Iwo amene amaphunzitsa malamulo sanandidziwe;
atsogoleri anandiwukira.
Aneneri ankanenera mʼdzina la Baala,
ndi kutsatira mafano achabechabe.
“Chifukwa chake Ine ndidzakuyimbaninso mlandu,”
akutero Yehova.
“Ndipo ndidzayimbanso mlandu zidzukulu zanu.
Pitani kumadzulo ku chilumba cha Kitimu, ndipo mukaone,
tumizani anthu ku Kedara kuti akafufuze bwino;
ndipo muona kuti zinthu zoterezi sizinachitikepo nʼkale lomwe:
Kodi ulipo mtundu wa anthu uliwonse umene unasinthapo milungu yake?
(Ngakhale kuti si milungu nʼkomwe).
Koma anthu anga asinthitsa Mulungu wawo waulemerero
ndi mafano achabechabe.
Inu mayiko akumwamba, dabwani ndi zimenezi,
ndipo njenjemerani ndi mantha aakulu,”
akutero Yehova.
“Popeza anthu anga achita machimo awiri:
Andisiya Ine
kasupe wa madzi a moyo,
ndi kukadzikumbira zitsime zawo,
zitsime zongʼaluka, zomwe sizingathe kusunga madzi.
Israeli si wantchito kapena kapolo wobadwira mʼnyumba, ayi.
Nanga nʼchifukwa chiyani amuwononga chotere?
Adani ake abangulira
ndi kumuopseza ngati mikango.
Dziko lake analisandutsa bwinja;
mizinda yake anayitentha popanda wokhalamo.
Ndiponso Aigupto a ku Mefisi ndi a ku Tapanesi
akuphwanyani mitu.
Zimenezitu zakuchitikirani
chifukwa munasiya Yehova Mulungu wanu
pamene Iye ankakutsogolerani pa njira yanu?
Tsopano mudzapindula chiyani mukapita ku Igupto,
kukamwa madzi a mu Sihori?
Ndipo mudzapindulanji mukapita ku Asiriya,
kukamwa madzi a mu mtsinje wa Yufurate?
Kuyipa kwanuko kudzakulangani;
kubwerera mʼmbuyo kwanuko kudzakutsutsani.
Tsono ganizirani bwino,
popeza ndi chinthu choyipa
kundisiya Ine Yehova Mulungu wanu;
ndi chinthu chowawa ndithu kusandiopa Ine Mulungu wanu.
Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
“Kuyambira kalekale inu munathyola goli lanu
ndi kudula msinga zanu;
munanena kuti, ‘Sitidzakutumikirani!’
Ndithudi, inu mwakhala ngati mkazi wachiwerewere.
Mukupembedza milungu ina pa phiri lililonse lalitali
ndiponso pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
Ine ndinakudzala iwe ngati mtengo wampesa wosankhika;
unali mpesa wabwino kwambiri ndi wodalirika.
Nanga nʼchifukwa chiyani wasanduka mpesa
wachabechabe wonga wa kutchire?
Ngakhale utasamba ndi soda
kapena kusambira sopo wambiri,
kuthimbirira kwa machimo ako kumaonekabe pamaso panga,”
akutero Ambuye Yehova.
“Iwe ukunena bwanji kuti, ‘Ine sindinadziyipitse;
sindinatsatire Abaala’?
Takumbukira mmene unkandichimwira mʼchigwa muja;
zindikira bwino zomwe wachita.
Iwe uli ngati ngamira yayikazi yaliwiro
yomangothamanga uku ndi uku,
wakhala ngati mbidzi yozolowera mʼchipululu,
yonka ninunkhiza pa nthawi yachisika.
Ndani angayiretse chilakolako chakecho?
Mphongo iliyonse yoyikhumba sidzavutika.
Pa nthawi yachisika chakecho mphongoyo idzayipeza.
Iwe usathamange, nsapato zingakuthere kuphazi
ndi kukhosi kwako kuwuma ndi ludzu.
Koma unati, ‘Zamkutu!
Ine ndimakonda milungu yachilendo,
ndipo ndidzayitsatira.’
“Monga momwe mbala imachitira manyazi pamene yagwidwa,
moteronso nyumba ya Israeli idzachita manyazi;
Aisraeliwo, mafumu ndi akuluakulu awo,
ansembe ndi aneneri awo.
Iwo amawuza mtengo kuti, ‘Iwe ndiwe abambo athu,’
ndipo amawuza mwala kuti, ‘Iwe ndiye amene unatibala.’
Iwo andifulatira Ine,
ndipo safuna kundiyangʼana;
Koma akakhala pa mavuto amati,
‘Bwerani mudzatipulumutse!’
Nanga ili kuti milungu yanu imene munadzipangira nokha?
Ibweretu ngati ingathe kukupulumutsani
pamene muli pamavuto!
Inu anthu a ku Yuda,
milungu yanu ndi yambiri kuchuluka kwake ngati mizinda yanu.
“Kodi mukundizengeranji mlandu?
Nonse mwandiwukira,”
akutero Yehova.
“Ine ndinalanga anthu ako popanda phindu;
iwo sanaphunzirepo kanthu.
Monga mkango wolusa,
lupanga lanu lapha aneneri anu.
“Inu anthu a mʼbado uno, ganizirani bwino mawu a Yehova:
“Kodi Ine ndinakhalapo ngati chipululu kwa Israeli
kapena ngati dziko la mdima wandiweyani?
Chifukwa chiyani anthu anga akunena kuti, ‘Ife tili ndi ufulu omayendayenda;
sitidzabweranso kwa Inu’?
Kodi namwali amayiwala zokongoletsera zake,
kapena kuyiwala zovala zake za ukwati?
Komatu anthu anga andiyiwala
masiku osawerengeka.
Mumadziwa bwino njira zopezera zibwenzi!
Choncho ngakhale akazi oyipa omwe mumawaphunzitsa njira zanu.
Ngakhale pa zovala zako anthu amapezapo
magazi a anthu osauka osalakwa.
Anthuwo simunawapeze akuthyola nyumba.
Komabe ngakhale zinthu zili chomwechi,
inu mukunena kuti, ‘Ndife osalakwa,
sadzatikwiyira.’
Ndidzakuyimbani mlandu
chifukwa mukunena kuti, ‘Ife sitinachimwe.’
Chifukwa chiyani
mukunkabe nimusinthasintha njira zanu?
Aigupto adzakukhumudwitsani
monga momwe Asiriya anakuchititsani manyazi.
Mudzachokanso kumeneko
manja ali kunkhongo.
Popeza Ine Yehova ndawakana anthu amene munkawadalira,
choncho sadzakuthandizani konse.
“Ngati munthu asudzula mkazi wake
ndipo mkaziyo nʼkuchoka nakakwatiwa ndi mwamuna wina,
kodi mwamuna woyambayo angathe kumutenganso mkaziyo?
Kodi atatero sindiye kuti dzikolo layipitsidwa kwambiri?
Koma iwe Israeli wachita zadama ndi zibwenzi zambiri.
Komabe bwerera kwa ine,”
akutero Yehova.
“Tayangʼana ku zitunda zowuma.
Kodi aliponso malo ena amene iwe sunachitepo zadama?
Iwe unkakhala mʼmbali mwa njira kumadikira zibwenzi zako,
ngati Mluya wobisalira anthu mʼchipululu.
Inu mwayipitsa dziko ndi zadama zanu
ndi ntchito zanu zoyipa.
Nʼchifukwa chake Yehova wayimitsa mvula,
ndipo mvula ya nthawi ya masika sinagwe.
Komabe uli ndi maonekedwe a mkazi wachiwerewere;
ndipo sukuchita manyazi ndi pangʼono pomwe.
Kodi iwe siposachedwa pomwepa pamene wanena
kuti, ‘Abambo anga, Inu bwenzi langa la unyamata wanga,
kodi mudzandikwiyira nthawi zonse?
Kodi ukali wanu udzakhalabe mpaka muyaya?’
Umu ndimo mmene umayankhulira,
koma umapitirizabe kuchita zoyipa monga momwe umathera.”
Kusakhulupirika kwa Israeli
Pa nthawi ya Mfumu Yosiya Yehova anandiwuza kuti, “Kodi waona zomwe Israeli wosakhulupirika uja wachita? Anakwera pa phiri lililonse lalitali ndi kupita pa tsinde pa mtengo uliwonse wogudira kukapembedza. Choncho anachita za chiwerewere kumeneko. Ndinaganiza kuti atachita zonsezi, adzabwerera kwa Ine, koma sanabwerere, ndipo mlongo wake wosakhulupirika uja, Yuda, anaziona zimenezi. Anaona kuti ndinasudzula Israeli wosakhulupirikayo ndi kumupirikitsa chifukwa cha zigololo zake. Komabe Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanaope, nayenso anapita kukachita chigololo. Chiwerewere cha Israeli chinali chochititsa manyazi kotero kuti chinayipitsa dziko lonse. Anachita chigololo popembedza mafano a miyala ndi mitengo. Israeli atachita zonsezi, Yuda mʼbale wake wosakhulupirika uja sanabwerere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma mwachiphamaso chabe,” akutero Yehova.
Yehova anandiwuza kuti, “Kusakhulupirika kwa Israeli nʼkochepa kuyerekeza ndi kusakhulupirika kwa Yuda. Pita ukalalikire kumpoto uthenga wakuti,
“ ‘Israeli wosakhulupirikawe, bwerera,’ akutero Yehova.
‘Sindidzakukalipira mpaka kalekale,
pakuti ndine wachifundo,’ akutero Yehova.
‘Sindidzakukwiyira mpaka kalekale.
Ungovomera kulakwa kwako
kuti unawukira Yehova Mulungu wako.
Vomera kuti unayendayenda kukapembedza milungu yachilendo
pansi pa mtengo uliwonse wogudira,
ndiponso kuti sunandimvere,’ ”
akutero Yehova.
“Bwererani, ana osakhulupirika, pakuti ndine mbuye wanu,” akutero Yehova. “Ndinakusankhani, mmodzimmodzi kuchokera ku mudzi uliwonse ndiponso awiriawiri kuchokera ku banja lililonse. Ndipo ndidzakupatsani abusa a pamtima panga amene adzakutsogolerani mwanzeru ndi mwaluntha. Masiku amenewo mukadzachulukana kwambiri mʼdzikomo, anthu sadzanenanso za ‘Bokosi la Chipangano la Yehova’ kapena kuliganizira. Sadzalikumbukiranso kapena kulifuna, ndipo sadzapanganso lina,”
akutero Yehova.
Nthawi imeneyo adzatcha Yerusalemu Mpando Waufumu wa Yehova, ndipo mitundu yonse ya anthu idzasonkhana mu Yerusalemu pamaso pa Yehova. Sadzawumiriranso kutsata mitima yawo yoyipa. Masiku amenewo fuko la Yuda lidzaphatikizana ndi fuko la Israeli, onse pamodzi adzachokera ku dziko la kumpoto kupita ku dziko limene ndinapatsa makolo awo, kuti likhale cholowa.
“Ine mwini ndinati,
“ ‘Ndikanakonda bwanji kukukhazikani pakati pa ana anga
ndikukupatsani dziko labwino kwambiri,
cholowa chokongola kwambiri kuposa cha mitundu ina ya anthu.’
Ndinaganiza kuti mudzanditcha Ine ‘Atate’
ndi kuti simudzaleka kunditsata.
Koma monga mkazi wosakhulupirika amasiya mwamuna wake,
momwemonso inu mwakhala osakhulupirika kwa Ine, inu fuko la Israeli,”
akutero Yehova.
Mawu akumveka pa magomo,
Aisraeli akulira ndi kupempha chifundo
chifukwa anatsata njira zoyipa
ndi kuyiwala Yehova Mulungu wawo.
Inu mukuti, “Bwererani, anthu osakhulupirika;
ndidzachiritsa kubwerera mʼmbuyo kwanu.”
“Inde, tidzabwerera kwa Inu
pakuti ndinu Yehova Mulungu wathu.
Ndithu kupembedza pa magomo
komanso kuchita maphwando pa mapiri zilibe phindu.
Zoonadi chipulumutso cha Israeli
chili mwa Yehova Mulungu wathu basi.
Kuyambira pa ubwana wathu milungu yochititsa manyazi ija yakhala ikutiwonongetsa phindu
la ntchito za makolo athu,
nkhosa ndi ngʼombe zawo,
ana awo aamuna ndi aakazi.
Tilekeni tigone pansi mwa manyazi,
ndipo kunyozeka kwathu kutiphimbe.
Paja tachimwira Yehova Mulungu wathu,
ife pamodzi ndi makolo athu
kuyambira nthawi ya ubwana wathu mpaka lero lino
sitinamvere Yehova Mulungu wathu.”
“Ngati mukufuna kubwerera, inu Aisraeli,
bwererani kwa Ine,”
akutero Yehova.
“Chotsani mafano anu onyansa pamaso panga
ndipo musasocherenso.
Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo
kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’
Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse
ndipo adzanditamanda.”
Zimene Yehova akunena kwa anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu ndi izi:
“Limani masala anu
musadzale pakati pa minga.
Dziperekeni nokha kwa Ine
kuti munditumikire ndi mtima wanu wonse,
inu anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu.
Muzichita zimenezi kuopa kuti mkwiyo wanga ungabuke ngati moto ndi kukutenthani,
chifukwa cha ntchito zanu zoyipazo
popanda wina wowuzimitsa.
Adani Ochokera Kumpoto kwa Yuda
“Lengeza ku Yuda ndi kulalikira mu Yerusalemu kuti,
‘Lizani lipenga mʼdziko lonse!’
Ndipo fuwulani kuti,
‘Sonkhanani!
Tiyeni tithawire ku mizinda yotetezedwa!’
Kwezani mbendera kuyangʼana ku Ziyoni!
Musachedwe, thawani kuti mupulumuke!
Pakuti Ine ndikubweretsa chilango kuchokera kumpoto,
kudzakhala chiwonongeko choopsa.”
Monga mkango umatulukira mʼngaka yake
momwemonso wowononga mayiko
wanyamuka ndi kutuluka ku mbuto yake.
Watero kuti awononge dziko lanu.
Mizinda yanu idzakhala mabwinja
popanda wokhalamo.
Choncho valani ziguduli,
lirani ndi kubuwula,
pakuti mkwiyo waukulu wa Yehova
sunatichokere.
“Pa tsiku limenelo, mfumu ndi nduna zake adzataya mtima,
ansembe adzachita mantha kwambiri,
ndipo aneneri adzathedwa nzeru,”
akutero Yehova.
Ndipo ine ndinati, “Haa, Ambuye Yehova, ndithu munawanyenga anthu awa pamodzi ndi Yerusalemu pamene munanena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’ chonsecho lupanga lili pakhosi pathu.”
Nthawi imeneyo anthu awa ndi Yerusalemu adzawawuza kuti, “Mphepo yotentha yochokera ku magomo a mʼchipululu ikuwomba pa anthu anga, osati mphepo yopeta kapena yoyeretsa; koma mphepo yamphamvu kwambiri yochokera kwa Ine. Tsono ndi Ineyo amene ndikuwaweruza.”
Taonani, adani akubwera ngati mitambo,
magaleta awo akubwera ngati kamvuluvulu,
akavalo awo ndi aliwiro kupambana chiwombankhanga.
Tsoka ilo! Tawonongeka!
Iwe Yerusalemu, tsuka mtima wako kuchotsa zoyipa kuti upulumuke.
Kodi maganizo ako oyipawo udzakhala nawo mpaka liti?
Pakuti amithenga akulalika mawu mʼdziko la Dani;
akulengeza za masautso kuchokera ku mapiri a Efereimu.
Iwo akuti, “Fotokozani zimenezi kwa anthu a mitundu ina,
lengezani zimenezi mu Yerusalemu kuti,
‘Ankhondo akubwera kuchokera ku dziko lakutali,
akufuwula ndi kudzazinga mizinda ya Yuda.
Azinga Yerusalemu ngati anthu olondera munda,
chifukwa Yerusalemu wandiwukira,’ ”
akutero Yehova.
“Makhalidwe anu ndi zochita zanu
zakubweretserani zimenezi.
Chimenechi ndiye chilango chanu.
Nʼchowawa kwambiri!
Nʼcholasa mpaka mu mtima!”
Mayo, mayo,
ndikumva kupweteka!
Aa, mtima wanga ukupweteka,
ukugunda kuti thi, thi, thi.
Sindingathe kukhala chete.
Pakuti ndamva kulira kwa lipenga;
ndamva mfuwu wankhondo.
Tsoka limatsata tsoka linzake;
dziko lonse lasanduka bwinja.
Mwadzidzidzi matenti athu awonongedwa,
mwa kanthawi kochepa nsalu zake zotchinga zagwetsedwa.
Kodi ndikhale ndikuona mbendera ya nkhondo,
ndi kumva kulira kwa lipenga mpaka liti?
Yehova akuti, “Anthu anga ndi zitsiru;
iwo sandidziwa.
Iwo ndi ana opanda nzeru;
samvetsa chilichonse.
Ali ndi luso lochita zoyipa,
koma sadziwa kuchita zabwino.”
Ndinayangʼana dziko lapansi,
ndipo linali lopanda anthu ndi lopanda kanthu;
ndinayangʼana thambo,
koma linalibe kuwala kulikonse.
Ndinayangʼana mapiri,
ndipo ankagwedezeka;
magomo onse ankangosunthira uku ndi uku.
Ndinayangʼana, ndipo sindinaone anthu;
mbalame iliyonse ya mlengalenga inali itathawa.
Ndinayangʼana, dziko lachonde linali litasanduka chipululu;
mizinda yake yonse inali itasanduka bwinja
pamaso pa Yehova, chifukwa cha mkwiyo wake.
Yehova akuti,
“Dziko lonse lidzasanduka chipululu
komabe sindidzaliwononga kotheratu.
Chifukwa chake dziko lapansi lidzalira
ndipo thambo lidzachita mdima,
pakuti ndayankhula ndipo sindidzafewa mtima,
ndatsimikiza ndipo sindidzabwerera mʼmbuyo.”
Pakumva phokoso la okwera pa akavalo ndi la anthu oponya mivi,
anthu a mʼmizinda adzathawa.
Ena adzabisala ku nkhalango;
ena adzakwera mʼmatanthwe
mizinda yonse nʼkuyisiya;
popanda munthu wokhalamo.
Iwe Yerusalemu, ndiwe bwinja!
Ukutanthauza chiyani kuvala zovala zofiira
ndi kuvalanso zokometsera zagolide?
Ngakhale udzikonze maso ako powapaka zokometsera,
ukungodzivuta chabe.
Zibwenzi zako zikukunyoza;
zikufuna kuchotsa moyo wako.
Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka,
kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba.
Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu.
Atambalitsa manja awo nʼkumati,
“Kalanga ife! Tikukomoka.
Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”
Palibe Munthu Wolungama
“Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu,
mudzionere nokha,
funafunani mʼmabwalo ake.
Ngati mungapeze munthu mmodzi
amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi,
ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.
Ngakhale anthu akulumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’
komabe akungolumbira mwachinyengo.”
Inu Yehova, kodi suja mumafuna anthu onena zoona?
Inu munawakantha anthuwo, koma sanamve kupweteka;
munawaphwanya anthuwo, koma sanatengepo phunziro.
Anawumitsa mitima yawo ngati mwala
ndipo anakaniratu kulapa.
Ndiye ndinati, “Awa ndi amphawi chabe;
anthu ochita zopusa.
Sadziwa njira ya Yehova,
sazindikira zimene Mulungu wawo amafuna.
Tsono ndidzapita kwa atsogoleri
ndi kukayankhula nawo;
ndithu iwo amadziwa njira ya Yehova,
amadziwa zomwe Mulungu wawo amafuna.”
Koma ayi, iwonso anathyola goli la Yehova
ndipo anadula msinga zawo.
Choncho mkango wochokera ku nkhalango udzawapha,
mmbulu wochokera ku thengo udzawawononga,
kambuku adzawabisalira pafupi ndi mizinda yawo
kuti akhadzule aliyense amene adzayesera kutuluka mʼmizindamo
pakuti kuwukira kwawo ndi kwakukulu
ndipo abwerera mʼmbuyo kwambiri.
Yehova akuti, “Kodi ndingakukhululukireni bwanji ndi zimene mwachita?
Ana anu andisiya Ine
ndipo amapembedza milungu imene si milungu konse.
Ine ndinawapatsa zonse zimene ankasowa,
komabe iwo anachita chigololo
namasonkhana ku nyumba za akazi achiwerewere.
Monga amachitira akavalo onenepa akamamemesa,
aliyense wa iwo ankathamangira mkazi wa mnzake.
Tsono ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?”
akutero Yehova.
“Kodi nʼkuleka kuwulipsira
mtundu woterewu?
“Pitani ku minda yake ya mipesa ndi kukayiwononga,
koma musakayiwononge kotheratu.
Sadzani nthambi zake
pakuti anthu amenewa si a Yehova.
Nyumba ya Israeli ndi nyumba ya Yuda
onse akhala osakhulupirika kotheratu kwa Ine.”
Iwowa ankanama ponena za Yehova kuti,
“Yehova sangachite zimenezi!
Choyipa sichidzatigwera;
sitidzaona nkhondo kapena njala.
Mawu a aneneri azidzangopita ngati mphepo;
ndipo mwa iwo mulibe uthenga wa Yehova.
Choncho zimene amanena zidzawachitikira okha.”
Chifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akuti,
“Popeza kuti anthu awa ayankhula mawu amenewa,
tsono mawu anga ndidzawasandutsa moto mʼkamwa mwako
ndipo anthu awa ndidzawasandutsa nkhuni zimene moto udzapserezeretu.
Inu Aisraeli,” Yehova akuti,
“Ndikukubweretserani mtundu wa anthu ochokera kutali,
ndi mtundu umene sunagonjetsedwepo,
mtundu wakalekale umene chiyankhulo chawo inu simuchidziwa,
zimene akunena inu simungazimvetse.
Zida zawo za nkhondo zapha anthu ambirimbiri;
onsewo ndi ankhondo amphamvu okhaokha.
Adzakudyerani zokolola zanu ndi chakudya chanu,
adzapha ana anu aamuna ndi aakazi;
adzakupherani nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu,
adzawononga mpesa wanu ndi mikuyu yanu.
Ndi malupanga awo adzagwetsa
mizinda yanu yotetezedwa imene mumayidalira.
“Komabe pa masiku amenewo sindidzakuwonongani kotheratu,” akutero Yehova. Ndipo pamene anthu adzafunsa Yehova kuti, “Chifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu wachita zimenezi?” Iwe udzawawuze kuti, “Monga momwe mwasiyira Ine ndi kutumikira milungu yachilendo mʼdziko mwanu, momwemonso mudzatumikira anthu a mʼdzikonso lachilendo.”
“Lengeza izi kwa ana a Yakobo
ndipo mulalikire kwa anthu a ku Yuda kuti,
Imvani izi, inu anthu opusa ndi opanda nzeru,
inu amene maso muli nawo koma simupenya,
amene makutu muli nawo koma simumva.
Kodi simuyenera kuchita nane mantha?”
Akutero Yehova.
“Kodi simuyenera kunjenjemera pamaso panga?
Ine ndinayika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
malire a muyaya amene nyanjayo singadutsepo.
Mafunde angawombe motani, koma sangathe kupitirira malirewo;
mafunde angakokome motani, koma sangadutse malirewo.
Koma anthu awa ndi nkhutukumve ndiponso a mitima yowukira;
andifulatira ndipo andisiyiratu.
Sananenepo mʼmitima mwawo kuti,
‘Tiyeni tizipembedza Yehova Mulungu wathu.
Kodi suja amatipatsa pa nthawi yake mvula yachizimalupsa ndi yamasika.
Iye salephera konse kutipatsa nyengo ya kholola.’
Koma zolakwa zanu zalepheretsa zonsezi;
ndipo machimo anu akumanitsani zabwino.
“Pakati pa anthu anga pali anthu ena oyipa
amene amabisalira anzawo monga amachitira mlenje mbalame
ndiponso ngati amene amatchera misampha kuti akole anthu anzawo.
Nyumba zawo zadzaza ndi chuma chochipeza mwa chinyengo
ngati zikwere zodzaza ndi mbalame.
Nʼchifukwa chake asanduka otchuka ndi olemera.
Ndipo ananenepa ndi kukhala ndi matupi osalala.
Ntchito zawo zoyipa nʼzopanda malire;
saweruza mwachilungamo nkhani ya ana amasiye kuti iyende bwino,
sateteza ufulu wa anthu osauka.
Kodi Ine ndingaleke kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
Kodi ndisawulipsire
mtundu woterewu?
Akutero Yehova.
“Chinthu chothetsa nzeru ndi choopsa kwambiri
chachitika mʼdzikomo:
Aneneri akunenera zabodza,
ndipo ansembe akuvomerezana nawo,
ndipo anthu anga akukonda zimenezi.
Koma mudzatani potsiriza?
Kuzingidwa kwa Yerusalemu
“Thawani, inu anthu a ku Benjamini!
Tulukani mu Yerusalemu!
Lizani lipenga ku Tekowa!
Kwezani mbendera ku Beti-Hakeremu!
Pakuti tsoka lalikulu likubwera kuchokera kumpoto,
ndipo chiwonongekocho nʼchachikulu.
Kodi mzinda wa Ziyoni suli ngati msipu wokongola kwambiri,
kumene abusa amafikako ndi ziweto zawo?
Abusa ndi nkhosa zawo adzabwera kudzalimbana nawo;
adzamanga matenti awo mowuzinga,
ndipo aliyense adzakhazika anthu ake pamalo pake.”
Adzanena kuti, “Konzekani kuwuthira nkhondo mzindawo!
Nyamukani, kuti tiwuthire nkhondo mzindawu masana ano.
Koma tili ndi tsoka, dzuwa lapendeka,
ndipo zithunzithunzi za kumadzulo zikunka zitalika.
Tsono nyamukani kuti tiwuthire nkhondo mzindawu usiku uno
ndi kuwononga malinga ake!”
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Dulani mitengo
ndipo mumange mitumbira yankhondo kulimbana ndi Yerusalemu.
Mzinda umenewu uyenera kulangidwa;
wadzaza ndi kuponderezana.
Monga momwe chitsime chimatulutsira madzi
ndi mmenenso Yerusalemu amatulutsira zoyipa zake.
Chiwawa ndi chiwonongeko ndi zomwe zimamveka mu mzindamo;
nthenda yake ndi mabala ake ndimaziona nthawi zonse.
Iwe Yerusalemu, tengapo phunziro,
kuopa kuti chikondi changa pa iwe chingakuchokere
ndi kusandutsa dziko lako kukhala bwinja
mopanda munthu wokhalamo.”
Yehova Wamphamvuzonse anandiwuza kuti,
“Adani adzawakunkha ndithu anthu otsala a Israeli,
monga momwe amachitira populula mphesa.
Tsono iwe yesetsa kupulumutsa amene ungathe
monga mmene amachitira munthu wokolola mphesa.”
Kodi ndiyankhule ndi yani ndi kumuchenjeza?
Ndinene mawu ochenjeza kwa yani kuti amve?
Makutu awo ndi otsekeka
kotero kuti sangathe kumva.
Mawu a Yehova ndi onyansa kwa iwo;
sasangalatsidwa nawo.
Koma ine ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,
ndipo ndatopa ndi kusunga mkwiyo wa Yehova.
Yehova anandiwuza kuti, “Tsono ndidzawutulutsira mkwiyo umenewu pa ana oyenda mʼmisewu
ndi pa achinyamata amene asonkhana pamodzi;
pakutinso mwamuna ndi mkazi wake adzatengedwa,
pamodzi ndi okalamba amene ali ndi zaka zochuluka.
Nyumba zawo adzazipereka kwa ena,
pamodzi ndi minda yawo ndi akazi awo.
Ndidzatambasula dzanja langa kukantha
anthu okhala mʼdzikomo,”
akutero Yehova.
“Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
onse ali ndi dyera lofuna kupeza phindu mwa kuba;
aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
onse amachita zachinyengo.
Amapoletsa zilonda za anthu anga
pamwamba pokha.
Iwo amanena kuti, ‘Mtendere, mtendere,’
pamene palibe mtendere.
Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazo?
Ayi, sachita manyazi ndi pangʼono pomwe;
sadziwa ndi kugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalange,”
akutero Yehova.
Yehova akuti,
“Imani pa mphambano ndipo mupenye;
kumeneko ndiye kuli njira zakale,
funsani kumene kuli njira yabwino. Yendani mʼmenemo,
ndipo mudzapeza mpumulo wa miyoyo yanu.
Koma inu munati, ‘Ife sitidzayenda njira imeneyo.’
Ine ndinakupatsani alonda oti akuyangʼanireni
ndipo ndinati, ‘Imvani kulira kwa lipenga!’
koma inu munati, ‘Sitidzamvera.’
Nʼchifukwa chake imvani, inu anthu a mitundu ina;
yangʼanitsitsani, inu amene mwasonkhana pano,
chimene chidzawachitikire anthuwo.
Imvani, inu anthu okhala pa dziko lapansi,
ndikubweretsa masautso pa anthu awa.
Zimenezi ndi mphotho ya ntchito zawo.
Iwowa sanamvere mawu anga
ndipo anakana lamulo langa.
Kodi pali phindu lanji ngakhale mubwere ndi lubani kuchokera ku Seba,
kapena zonunkhira zina kuchokera ku dziko lakutali?
Nsembe zanu zopsereza Ine sindidzalandira;
nsembe zanu sizindikondweretsa.”
Choncho Yehova akuti,
“Ndidzayika zokhumudwitsa pamaso pa anthu awa.
Abambo ndi ana awo aamuna onse adzapunthwa ndi kugwa;
anansi awo ndi abwenzi awo adzawonongeka.”
Yehova akunena kuti,
“Taonani, gulu lankhondo likubwera
kuchokera kumpoto;
mtundu wa anthu amphamvu wanyamuka
kuchokera kumathero a dziko lapansi.
Atenga mauta ndi mikondo;
ndi anthu ankhanza ndi opanda chifundo.
Phokoso lawo lili ngati mkokomo wa nyanja.
Akwera pa akavalo awo
ndipo akonzekera ngati anthu ankhondo,
kudzakuthirani nkhondo anthu a ku Ziyoni.”
A ku Ziyoni akuti “Ife tamva mbiri yawo,
ndipo manja anthu alefukiratu.
Nkhawa yatigwira,
ndipo tikumva ululu ngati mayi pa nthawi yake yochira.
Musapite ku minda
kapena kuyenda mʼmisewu,
pakuti mdani ali ndi lupanga,
ndipo ponseponse anthu akuchita mantha.
Inu anthu anga, valani ziguduli
ndipo gubudukani pa phulusa;
lirani mwamphamvu
ngati munthu wolirira mwana wake mmodzi yekha,
pakuti mwadzidzidzi wowonongayo
adzabwera kudzatipha.
“Iwe Yeremiya, ndakuyika kuti ukhale choyesera zitsulo.
Uwayese anthu anga
monga ungayesere chitsulo
kuti uwone makhalidwe awo.
Onsewo ali ndi khalidwe lokanika ndi lowukira
ndipo akunka nanena zamiseche.
Iwo ndi olimba ngati mkuwa ndi chitsulo.
Onse amangochita zoyipa zokhazokha.
Moto mu mvukuto ukuyaka kwambiri;
mtovu watha kusungunuka ndi moto.
Koma ntchito yosungunulayo sikupindula
chifukwa zoyipa sizikuchokapo.
Iwo ali ngati siliva wotayidwa,
chifukwa Yehova wawakana.”
Chipembedzo Chabodza Nʼchopanda Phindu
Mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeremiya ndi awa, “Ima pa chipata cha Nyumba ya Yehova ndipo kumeneko ukalalikire uthenga uwu:
“ ‘Imvani mawu a Yehova, inu nonse anthu a ku Yuda amene mumalowa pa chipata ichi kudzapembedza Yehova. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Konzani makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndipo ndidzakulolani kukhala pa malo ano. Musamakhulupirire mawu anu achinyengo onena kuti, ‘Ino ndi Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova, Nyumba ya Yehova!’ Ngati mutasinthadi makhalidwe anu ndi zochita zanu, ndi kumachitirana zolungama, ngati mutaleka kuzunza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye ndi kuleka kupha anthu osalakwa pa malo ano, ndipo ngati muleka kutsatira milungu ina, kuti ingakuwonongeni, Ine ndidzakulolani kukhala pa malo ano, mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu mpaka muyaya. Koma onani, inu mukudalira mawu abodza amene alibe phindu.
“Kodi inu muziba ndi kupha, kuchita chigololo ndi kulumbira monama, kufukiza lubani kwa Baala ndi kutsatira milungu ina imene simunayidziwe, ndipo kenaka nʼkubwera kudzayima pamaso panga mʼNyumba ino, Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langa, inu nʼkumati, ‘Tapulumuka.’ Mwapulumuka kuti muzichitabe zonyansazi? Kodi Nyumba ino imene imadziwika ndi Dzina langa, yasanduka phanga la anthu olanda zinthu anzawo mwachifwamba inu mukuona? Komatu ndakhala ndi kuziona zonsezi! akutero Yehova.”
“ ‘Pitani tsopano ku malo anga ku Silo, malo amene poyamba ankadziwika ndi Dzina langa, ndipo mukaone zimene ndinachita kumeneko chifukwa cha kuyipa kwa anthu anga Aisraeli. Tsono popeza munkachita zonsezi, ngakhale Ine kukuyankhulani koma inu osamvera, kukuyitanani koma inu osayankha, choncho ndidzachita pa Nyumba imene imadziwika ndi Dzina langayi, Nyumba ya Yehova imene mumayidalira, malo amene ndinapereka kwa inu ndi makolo anu, zomwe ndinachita ku Silo. Ndidzakuthamangitsani pamaso panga, ngati momwe ndinachitira abale anu onse, anthu a Efereimu.’ ”
“Choncho iwe Yeremiya usawapempherere anthu awa ngakhale kuwapepesera kapenanso kuwapembedzera; usandidandaulire, chifukwa Ine sindidzakumvera. Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? Ana akutorera nkhuni, abambo akusonkha moto, ndipo amayi akukanda ufa kuti aphike makeke oti akapereke nsembe kwa mfumukazi yazakumwamba. Iwo amathira nsembe ya zakumwa kwa milungu ina kuti andipsetse mtima. Koma kodi akuvutitsa Ine? Kodi sakungodzivuta okha, ndi kudzichititsa manyazi? akutero Yehova.”
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Ndidzatsanulira mkwiyo wanga pa Nyumba yangayi, anthu, nyama, mitengo ndi zipatso zomwe. Mkwiyowo udzakhala ngati moto wosazimitsika.
“Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Wonjezerani nsembe zanu zopsereza pa nsembe zanu zinazo ndipo mudye nyama yakeyo! Pakuti pamene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto ndi kuyankhula nawo, sindinawalamulire kuti azipereka nsembe zopsereza kapena nsembe zinazo, koma ndinawalamula kuti: Mverani Ine, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu ndipo inu mudzakhala anthu anga. Muzitsata zonse zimene ndakulamulirani, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Koma anthuwo sanamvere kapena kulabadira; mʼmalo mwake anapitirira kusamvera ndi mitima yawo yoyipa. Iwo anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo. Kuyambira tsiku limene makolo awo anachoka ku Igupto mpaka lero lino, ndakhala ndikuwatumizira atumiki anga, aneneri. Koma anthuwo sanandimvere kapena kusamalira. Anawumitsa mitima yawo ndi kuchita zoyipa kuposa makolo awo.
“Ngakhale iwe uwawuze zonsezi koma sadzakumvera. Ngakhale uwayitane koma sadzakuyankha. Nʼchifukwa chake udzawawuze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere Yehova Mulungu wake, wosalola kulangizidwa. Choonadi chatha; chazimirira pa milomo yawo.’
“Tsono meta tsitsi lako ndi kulitaya. Ulire kwambiri pa zitunda zopanda zomera, pakuti Yehova waukana ndi kuwusiya mʼbado umene wamukwiyitsawu.”
Chigwa cha Imfa
“Anthu a ku Yuda achita zoyipa pamaso panga, akutero Yehova. Ayimika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi Dzina langa ndipo ayipitsa. Amanga nsanja yopembedzera Tofeti mʼChigwa cha Hinomu kuti apserezereko ana awo aamuna ndi aakazi. Zimenezi Ine sindinawalamulire ngakhale kuziganizira nʼkomwe. Nʼchifukwa chake masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzawatchulanso malowo Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma adzawatchula Chigwa cha Imfa, chifukwa adzakwirira anthu akufa ku Tofeti mpaka osapezekanso malo owayika. Ndipo mitembo ya anthu amenewa idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo, ndipo palibe wina amene adzazipirikitse. Ndidzathetsa nyimbo zonse zachisangalalo ndi zachikondwerero mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu. Sikudzamvekanso mawu a chikondwerero a mkwatibwi ndi mkwati pakuti dzikolo lidzasanduka chipululu.”
Yehova akuti, “ ‘Pa nthawi imeneyo, mafupa a mafumu ndi a akuluakulu a ku Yuda, mafupa a ansembe ndi a aneneri, ndiponso mafupa a anthu a ku Yerusalemu adzafukulidwa. Adzawamwaza pa nthaka kuyangʼana dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zonse zamlengalenga, zimene ankazikonda, kuzitumikira ndi kuzitsatira, kupemphako nzeru ndiponso kuzilambira. Mafupawo sadzawasonkhanitsa kapena kuwakwirira, koma adzakhala ngati ndowe pamwamba pa nthaka. Otsala onse a mtundu woyipawu adzafuna imfa kopambana moyo kulikonse kumene ndidzawapirikitsirako, akutero Yehova Wamphamvuzonse.’ ”
Tchimo ndi Chilango Chake
“Tsono awuze anthuwa, ‘Yehova akuti:
“ ‘Kodi anthu akagwa sangadzukenso?
Munthu akasochera kodi sangathe kubwereranso?
Chifukwa chiyani nanga anthu awa akupitirirabe kuchimwa, osabwerera?
Chifukwa chiyani Yerusalemu akubwerera mʼmbuyo?
Iwo akangamira chinyengo;
akukana kubwerera.
Ine ndinatchera khutu kumvetsera
koma iwo sanayankhulepo zoona.
Palibe woyipa amene analapapo zoyipa zake,
nʼkumati, ‘Ine ndachita chiyani?’
Aliyense akutsatira njira yake
ngati kavalo wothamangira nkhondo.
Mbalame yotchedwa kakowa ija imadziwa
nthawi yake mlengalenga.
Koma nkhunda, namzeze ndi chingalu
zimadziwa nthawi yonyamukira ulendo,
koma anthu anga sadziwa
malamulo a Yehova.
“ ‘Inu mukunena bwanji kuti,
‘Ndife anzeru ndipo timasunga malamulo a Yehova?’
Koma ndi alembi anu
amene akulemba zabodza.
Anthu anzeru achita manyazi;
athedwa nzeru ndipo agwidwa.
Iwo anakana mawu a Yehova.
Nanga tsono nzeru zawo ziwapinduliranji?
Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena
ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse.
Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,
onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba.
Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe,
onse amachita zachinyengo.
Iwo amapoletsa zilonda za anthu anga
pamwamba chabe
nʼkumati, ‘Mtendere, mtendere,’
pamene palibe mtendere.
Kodi amachita manyazi akamachita zonyansazi?
Ayi, alibe manyazi ndi pangʼono pomwe;
iwo sadziwa nʼkugwetsa nkhope komwe.
Choncho iwo adzagwera pakati pa anzawo amene agwa kale;
adzagwa pansi tsiku limene ndidzawalanga,
akutero Yehova.
“ ‘Ndidzatenga zokolola zawo,
Sipadzakhalanso mphesa pa mpesa
kapena nkhuyu pa mkuyu,
ndipo masamba ake adzawuma.
Zinthu zimene ndinawapatsa
ndidzawachotsera.’ ”
Koma amati, “Tikukhala pano chifukwa chiyani?
Tiyeni tonse pamodzi
tithawire ku mizinda yotetezedwa
ndi kukafera kumeneko.
Pakuti Yehova Mulungu wathu watsimikiza kuti tiyenera kufa.
Watipatsa madzi aululu kuti timwe,
chifukwa tamuchimwira.
Tinkayembekezera mtendere
koma palibe chabwino chomwe chinachitika,
tinkayembekezera kuchira
koma tinakumana ndi zoopsa zokhazokha.
Kulira kwa ngʼombe zazimuna za mdani
kukumveka kuchokera ku Dani;
dziko lonse likunjenjemera
chifukwa cha kulira kwa akavalowo.
Akubwera kudzawononga dziko
ndi zonse zimene zili mʼmenemo.
Adzawononga mzinda ndi onse okhalamo.”
Yehova akuti, “Onani, ndikukutumizirani njoka zaululu,
mphiri zimene munthu sangathe kuzilodza,
ndipo zidzakulumani,”
Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri,
mtima wanga walefukiratu.
Imvani kulira kwa anthu anga
kuchokera ku dziko lakutali:
akuti, “Kodi Yehova sali ku Ziyoni?
Kodi mfumu yake sili kumeneko?”
“Chifukwa chiyani akundiputa ndi mafano awo osema,
ndi milungu yawo yachilendo?”
“Nthawi yokolola yapita,
chilimwe chapita,
koma sitinapulumuke.”
Chifukwa cha mavuto a anthu anga, ine ndikumva kuwawa;
ndikungolira ndipo mantha aakulu andigwira.
Kodi ku Giliyadi kulibe mankhwala ochiritsa?
Kodi kumeneko kulibe singʼanga?
Nanga chifukwa chiyani mabala
a anthu anga sanapole?
Aa, ndikanakonda kuti mutu wanga ukanakhala chitsime cha madzi,
ndi maso anga ngati kasupe wa misozi!
Ndikanalira usana ndi usiku
kulirira anthu anga amene aphedwa.
Ndani adzandipatsa malo
ogona mʼchipululu
kuti ndiwasiye anthu anga
ndi kuwachokera kupita kutali;
pakuti onse ndi achigololo,
ndiponso gulu la anthu onyenga.
“Amapinda lilime lawo ngati uta.
Mʼdzikomo mwadzaza
ndi mabodza okhaokha
osati zoonadi.
Amapitirirabe kuchita zoyipa;
ndipo sandidziwa Ine.”
Akutero Yehova.
“Aliyense achenjere ndi abwenzi ake;
asadalire ngakhale abale ake.
Aliyense amafuna kumudyera mʼbale wake masuku pa mutu.
Choncho aliyense amachitira bwenzi lake ugogodi.
Aliyense amamunamiza mʼbale wake
ndipo palibe amene amayankhula choonadi.
Anapazoloweza pakamwa pawo kunena zabodza;
amalimbika kuchita machimo.
Iwe wakhalira mʼchinyengo
ndipo ukukana kundidziwa Ine,”
akutero Yehova.
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, Ine ndidzawasungunula ngati chitsulo ndi kuwayesa.
Kodi ndingachite nawonso
bwanji chifukwa cha machimo awo?
Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa;
limayankhula zachinyengo.
Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake,
koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.
Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi?
akutero Yehova.
‘Kodi ndisawulipsire
mtundu wotere wa anthu?’ ”
Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri
ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu.
Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako,
ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe.
Mbalame zamlengalenga zathawa
ndipo nyama zakuthengo zachokako.
Ndipo Yehova anati, “Ndidzasandutsa Yerusalemu kukhala bwinja,
malo okhalamo ankhandwe;
ndipo ndidzawononga mizinda ya Yuda
kotero kuti palibe munthu amene adzakhalemo.”
Ine ndinati, “Kodi munthu wanzeru ndani woti nʼkumvetsa zimenezi? Kodi ndani amene Yehova anayankhula naye zimenezi kuti akafotokozere ena? Nʼchifukwa chiyani dziko lawonongeka ndi kusanduka chipululu, mʼmene anthu sadutsamo?”
Yehova anati, “Nʼchifukwa chakuti anthuwa analeka kutsata malamulo anga amene ndinawapatsa; sanandimvere kapena kuwasamala. Mʼmalo mwake, anatsatira zolakwa za mʼmitima yawo; anapembedza Abaala ngati momwe makolo awo anawaphunzitsira.” Tsono chimene Ine Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli ndidzachite ndi anthu amenewa ndi ichi: “Ndidzawadyetsa chakudya cha ziphe ndi kuwamwetsa madzi a ndulu. Ndidzawabalalitsa pakati pa mitundu ya anthu imene iwowo kapena makolo awo sanayidziwe, ndipo ndidzawalondola ndi ankhondo mpaka nditawawononga.”
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Tsopano ganizirani! Muyitane akazi olira mwachisoni kuti abwere;
itanani akazi odziwa kulira bwino.”
Anthu akuti, “Abwere mofulumira
kuti adzatilire
mpaka mʼmaso mwathu mutatuluka misozi
ndi kuti msidze zathu zinyowe ndi madzi.
Kulira mwachisoni kukumveka kuchokera mu Ziyoni akuti,
‘Aa! Ife tawonongeka!
Tachita manyazi kwambiri!
Tiyenera kuchoka mʼdziko lathu
chifukwa atipirikitsa mʼnyumba zathu.’ ”
Tsono inu amayi, imvani mawu a Yehova;
tcherani makutu anu kuti mumve mawu a Yehova.
Phunzitsani ana anu aakazi kulira mwachisoni;
aliyense aphunzitse mnzake nyimbo ya maliro.
Imfa yatifikira kudzera mʼmazenera athu
ndipo yalowa mʼnyumba zathu zotetezedwa;
yapha ana athu mʼmisewu,
ndi achinyamata athu mʼmabwalo.
Yehova anandiwuza kuti ndinene izi kuti,
“ ‘Mitembo ya anthu
idzakhala ili lambalamba ngati ndowe mʼminda,
ngati mapesi mʼmbuyo mwa wokolola,
popanda munthu woyitola.’ ”
Yehova akuti,
“Munthu wanzeru asanyadire nzeru zake,
kapena munthu wamphamvu kunyadira nyonga zake,
kapena munthu wolemera kunyadira chuma chake,
koma ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire chinthu ichi:
kuti iye amamvetsa za Ine ndipo amandidziwa,
kuti ndine Yehova, amene ndimakonda chifundo,
chilungamo ndiponso ungwiro pa dziko lapansi.
Zimenezi ndizo ndimakondwera nazo,”
akutero Yehova.
“Nthawi ikubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzalanga onse amene anachita mdulidwe koma mu mtima sasamala nʼkomwe. Ndidzalanga anthu a ku Igupto, Yuda, Edomu, Amoni, Mowabu, ndiponso onse amene amakhala kutali ku chipululu. Mitundu ina yonseyi ndi yosachita mdulidwe, ngakhalenso Aisraeli nawonso sanachite mdulidwe wa mu mtima.”
Mulungu ndi Mafano
Inu Aisraeli, imvani zimene Yehova akunena. Yehova akuti,
“Musatsatire makhalidwe a anthu a mitundu ina
kapena kuchita mantha ndi zizindikiro zamlengalenga,
ngakhale anthu a mitundu ina amachita nazo mantha.
Pakuti miyambo ya mitundu inayo ndiyachabechabe.
Iwo amakadula mtengo ku nkhalango
ndipo mmisiri amawusema ndi sompho.
Amakongoletsa chosemacho ndi siliva ndi golide;
kenaka amachikhomerera ndi misomali
kuti chisagwedezeke.
Mafano awo ali ngati mtengo wakanjedza woopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka.
Mafanowo sangathe nʼkuyankhula komwe
ndipo ayenera kunyamulidwa
popeza sangathe nʼkuyenda komwe.
Musachite nawo mantha
popeza sangathe kukuchitani choyipa
ndiponso alibe mphamvu yochitira chabwino chilichonse.”
Palibe wofanana nanu, Inu Yehova;
Inu ndinu wamkulu,
ndipo dzina lanu lili ndi mphamvu yayikulu.
Ndani amene angaleke kukuopani,
inu Mfumu ya mitundu ya anthu?
Chimenechi ndicho chokuyenerani.
Pakati pa anthu anzeru onse komanso mafumu onse
a mitundu ya anthu,
palibe wina wofanana nanu.
Onsewo ndi opusa ndi opanda nzeru;
malangizo awo amawatenga kuchokera kwa mafano achabechabe opanga ndi mitengo.
Siliva wosula amabwera naye kuchokera ku Tarisisi
ndipo golide amachokera naye ku Ufazi.
Mafanowo ndi ntchito ya anthu aluso ndi odziwa kuzokota golide.
Tsono mafanowo amawaveka zovala za mtundu wamtambo ndi pepo.
Yonseyo ndi ntchito ya anthu a luso.
Koma Yehova ndiye Mulungu woona;
Iyeyo ndiye Mulungu wamoyo, Mfumu yamuyaya.
Akakwiya, dziko limagwedezeka;
anthu a mitundu ina sangathe kupirira ukali wakewo.
“Awuze anthu awa kuti, ‘Milungu iyi, imene sinalenge dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, idzawonongeka pa dziko lapansi ndi pansi pa thambo.’ ”
Koma Mulungu analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
ndipo anayala thambo mwaluso lake.
Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba;
Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene osungirako.
Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
alibe moyo mʼkati mwawo.
Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
Pamene anthuwo azidzaweruzidwa, mafanowo adzawonongedwa.
Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse
kuphatikizapo Israeli, mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Chiwonongeko Chikubwera
Sonkhanitsani katundu wanu,
inu amene mukukhala mʼlinga la ankhondo.
Pakuti Yehova akuti,
“Tsopano Ine ndidzachotsa anthu onse
amene akukhala mʼdziko lino;
adzakhala pa mavuto
mpaka adzamvetsa.”
Aliyense ankangoti, “Mayo ine, chifukwa cha kupweteka kwanga!
Chilonda changa nʼchachikulu!”
Koma ine ndinkaganiza kuti, “Ndithu, ili ndi vuto langa basi,
choncho ndingolipirira.”
Tenti yanga yawonongeka,
zingwe zake zonse zaduka.
Ana anga andisiya ndipo kulibenso.
Palibenso amene adzandimangire tenti,
kapena kufunyulula nsalu yake.
Abusa ndi opusa
ndipo sanapemphe nzeru kwa Yehova;
choncho palibe chimene anapindula
ndipo nkhosa zawo zonse zabalalika.
Tamvani! kukubwera mphekesera,
phokoso lalikulu la gulu la a ankhondo likumveka kuchokera kumpoto!
Lidzasandutsa bwinja mizinda ya ku Yuda,
malo okhala nkhandwe.
Pemphero la Yeremiya
Inu Yehova, ndikudziwa kuti moyo umene munthu ali nawo si wake;
munthuyo sangathe kuwongolera mayendedwe ake.
Inu Yehova, langizeni, komatu mwachilungamo,
osati ndi mkwiyo wanu,
mungandiwononge kotheratu.
Tsanulirani ukali wanu pa mitundu ya anthu amene sakudziwani,
ndiye kuti mitundu ya anthu amene satama pa dzina lanu mopemba.
Iwo aja anasakaza Yakobo;
amusakaza kotheratu
ndipo awononga dziko lake.
Pangano Liphwanyidwa
Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Imvani mawu a pangano ili, ndipo uwawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Awuze kuti Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ‘adzakhala wotembereredwa munthu amene samvera mawu a pangano ili. Awa anali mawu amene ndinalamulira makolo anu nditawatulutsa mu Igupto, kuchoka mʼngʼanjo yamoto.’ Ine ndinati, ‘Mverani Ine ndi kuchita chilichonse chimene ndakulamulirani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.”
Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.”
Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira. Kuyambira nthawi imene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto mpaka lero, ndakhala ndi kuwachenjeza kawirikawiri kuti, ‘Mverani Ine.’ Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ”
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu andiwukira. Abwereranso ku machimo a makolo awo, amene anakana kumvera mawu anga. Akutsata milungu ina ndi kumayitumikira. Aisraeli ndi Ayuda aphwanya pangano limene ndinachita ndi makolo awo. Choncho Yehova akuti, ‘Ndidzawagwetsera mavuto amene sadzatha kuwalewa. Ngakhale adzandilirire, sindidzawamvera. Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika. Iwe Yuda, uli ndi milungu yochuluka ngati chiwerengero cha mizinda yako; chiwerengero cha maguwa ansembe amene umafukizirapo lubani kwa Baala chili ngati misewu ya mu Yerusalemu.’
“Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.
“Kodi anthu anga okondedwa akudzachita chiyani mʼNyumba yanga?
Kodi suja iwowa amachita zoyipa zambiri?
Kodi mungathe kupulumuka,
tsoka osakugwerani
chifukwa cha nsembe zanuzo?”
Kale Yehova ankakutchani mtengo wa olivi wa masamba obiriwira,
wokhala ndi zipatso zokongola.
Koma tsopano adzawutentha
ndi mkuntho wamkokomo
ndipo nthambi zake zidzapserera.
Yehova Wamphamvuzonse, amene anakudzalani, walamula kuti mavuto akugwereni. Inu a banja la Yuda ndi a banja la Israeli munachitira Yehova zoyipa ndi kumukwiyitsa pamene munkapereka nsembe zanu kwa Baala.
Amuchitira Chiwembu Yeremiya
Yehova anandiwululira ndipo ndinadziwa. Iye anatsekula maso anga kuti ndione chiwembu chawocho. Ndinali ngati mwana wankhosa wofatsa amene akupita naye kukamupha; sindinkadziwa kuti chiwembu chimene ankakonzekeracho chinkaloza ine. Iwo amati:
“Tiyeni timuphe
munthu ameneyu
kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”
Koma, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumaweruza molungama
ndi kuyesa mitima ndi maganizo,
lolani kuti ine ndione kuti mwawalipsira,
pakuti mlandu wanga ndawupereka mʼmanja mwanu.
“Nʼchifukwa chake Yehova akunena za anthu a ku Anatoti amene akufuna kuwononga moyo wako namanena kuti, ‘Usanenere mʼdzina la Yehova, ukatero ife tidzakupha ndi manja athu,’ koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzawalanga. Achinyamata awo adzaphedwa ndi lupanga, ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala. Sipadzakhala otsala ndi mmodzi yemwe, chifukwa ndidzalanga anthu a ku Anatoti chikadzafika chaka chawo cha chilango.’ ”
Madandawulo a Yeremiya
Yehova, Inu mumakhala wokhoza nthawi zonse
ndikati nditsutsane nanu.
Komabe ndikufuna kuyankhula nanu za mlandu wanga.
Chifukwa chiyani anthu oyipa zinthu zimawayendera bwino?
Chifukwa chiyani anthu achinyengo amakhala pabwino?
Inu munawadzala ndipo anamera mizu;
amakula ndi kubereka zipatso.
Dzina lanu limakhala pakamwa pawo nthawi zonse,
koma mitima yawo imakhala kutali ndi Inu.
Koma Inu Yehova, ine mumandidziwa;
mumandiona ndipo mumayesa zolingalira zanga.
Akokeni anthu oyipawo ngati nkhosa zokaphedwa!
Ayikeni padera mpaka tsiku loti akaphedwe!
Kodi dziko lidzakhala likulirabe mpaka liti
ndipo udzu mʼmunda uliwonse udzakhalabe ofota mpaka liti?
Nyama ndi mbalame kulibiretu
chifukwa anthu amene amakhalamo ndi oyipa.
Iwo amati:
“Yehova sangathe kuona ntchito zathu.”
Yankho la Mulungu
Yehova anayankha kuti, “Ngati kukutopetsa kuthamanga pamodzi ndi anthu
nanga ungapikisane bwanji ndi akavalo?
Ngati ukupunthwa ndi kugwa pa malo abwino,
udzatha bwanji kuthamanga mʼnkhalango
za ku Yorodani?
Ngakhale abale ako
ndi anansi akuwukira,
onsewo amvana zokuyimba mlandu.
Usawakhulupirire,
ngakhale ayankhule zabwino ndi iwe.
“Ine ndawasiya anthu anga;
anthu amene ndinawasankha ndawataya.
Ndapereka okondedwa anga
mʼmanja mwa adani awo.
Anthu amene ndinawasankha
asanduka ngati mkango wa mʼnkhalango.
Akundibangulira mwaukali;
nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawo.
Anthu anga amene ndinawasankha
asanduka ngati mbalame yolusa yamawangamawanga
imene akabawi ayizinga.
Pitani, kasonkhanitseni nyama zakuthengo.
Mubwere nazo kuti zidzadye mbalameyo.
Abusa ambiri anawononga munda wanga wa mpesa,
anapondereza munda wanga;
munda wanga wabwino uja
anawusandutsa chipululu.
Unawusandutsadi chipululu.
Ukanali wokhawokha chomwecho ukundilirira Ine.
Dziko lonse lasanduka chipululu
chifukwa palibe wolisamalira.
Anthu onse owononga abalalikira
ku zitunda zonse za mʼchipululu.
Yehova watuma ankhondo ake
kudzawatha kuyambira kumalire ena a dziko mpaka ku malire enanso a dziko,
ndipo palibe amene adzakhale pa mtendere.
Anthu anafesa tirigu koma anatuta minga;
anadzitopetsa kugwira ntchito koma osapeza phindu lililonse.
Choncho mudzachita manyazi ndi zokolola zanu
chifukwa cha mkwiyo wa Yehova.”
“Anthu oyipa oyandikana ndi anthu anga Aisraeli, akuwalanda Aisraeliwo dziko, cholowa chimene ndinawapatsa. Nʼchifukwa chake ndidzawachotsa mʼdziko limenelo, ndipo ndidzachotsa banja la Yuda pakati pawo. Komabe nditawachotsa, ndidzawachitiranso chifundo, ndipo ndidzabwezera aliyense cholowa chake ndi dziko lake. Ndipo ngati iwo adzaphunzira bwino njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa, namanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo,’ monga iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, Ine ndidzawakhazikitsa pakati pa anthu anga. Koma ngati mtundu wina uliwonse sudzamvera, Ine ndidzawuchotsa ndi kuwuwonongeratu,” akutero Yehova.
Lamba Womanga Mʼchiwuno
Yehova anandiwuza kuti, “Pita kagule lamba wansalu yosalala ndipo ukavale mʼchiwuno mwako, koma usakamuviyike mʼmadzi.” Choncho ndinakagula lambayo, monga momwe anandiwuzira Yehova, ndipo ndinamanga mʼchiwuno mwanga.
Kenaka Yehova anandiyankhulanso kachiwiri kuti, “Tenga lamba amene unagula ndi kuvala mʼchiwuno mwako uja. Tsono pita ku mtsinje wa Yufurate ndipo ukamubise lambayo mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.” Ndipo ndinapitadi ndi kukabisa lambayo ku Yufurate, monga anenera Yehova.
Patapita masiku ambiri Yehova anandiwuzanso kuti, “Pitanso ku Yufurate ndipo ukatenge lamba amene ndinakuwuza kuti ukamubise kumeneko.” Choncho ndinapita ku Yufurate kukafukula lambayo ndi kumuchotsa pamalo pamene ndinamubisa, koma nthawi imeneyi nʼkuti lambayo atawonongeka kotheratu ndipo analibenso ntchito.
Pamenepo Yehova anandiwuza kuti, “Izi ndi zimene ine ndikunena: ‘Umu ndi mmene ndidzawonongere zimene akunyadira kwambiri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Anthuwa ndi oyipa. Iwo akana kumvera mawu anga. Mʼmalo mwake amawumirira kutsata milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Anthu amenewa adzakhala ngati lamba wopanda ntchitoyu. Monga momwe lamba amakanirira mʼchiwuno cha munthu, momwemonso ndinakonza kuti nyumba yonse ya Israeli ndi nyumba yonse ya Yuda indikangamire Ine kuti akhale anthu anga, kuti azitamanda dzina langa ndi kulemekeza Ine. Koma iwo sanamvere,’ akutero Yehova.
Zikopa Zothiramo Vinyo
“Awuze anthuwo kuti, ‘Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Mtsuko uliwonse adzawudzaza ndi vinyo.’ Ndipo ngati iwo anena kwa iwe kuti, ‘Kodi ngati ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse udzadzazidwa ndi vinyo?’ Tsono iwe uwawuze kuti, Yehova akuti ‘Ine ndidzaledzeretsa anthu onse okhala mʼdziko muno, kuyambira mafumu amene amakhala pa mpando waufumu wa Davide, ansembe, aneneri, pamodzi ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. Ndidzawagundanitsa mitu kuti aphwanyane okhaokha ngati mitsuko, makolo ndi ana awo, akutero Yehova. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo kapena kukhudzidwa nawo kuti ndileke kuwawononga.’ ”
Yuda Adzapita ku Ukapolo
Imvani inu Aisraeli ndipo tcherani khutu,
musadzitukumule,
pakuti ndi Yehova amene akuyankhula.
Lemekezani Yehova Mulungu wanu
asanagwetse mdima,
mapazi anu asanayambe kupunthwa
mʼchisisira chamʼmapiri.
Asanasandutse kuwala
mukuyembekezerako kukhala
mdima wandiweyani.
Koma ngati simumvera,
ndidzalira kwambiri
chifukwa cha kunyada kwanu.
Mʼmaso mwanga
mwadzaza ndi misozi yowawa
chifukwa nkhosa za Yehova zatengedwa ukapolo.
Uza mfumu pamodzi ndi amayi ake kuti,
“Tsikani pa mipando yaufumuyo,
pakuti zipewa zanu zaufumu zokongolazo
zagwa pansi.”
Mizinda ya ku Negevi yatsekedwa
ndipo palibe wina woti nʼkuyitsekula.
Yuda yense watengedwa kupita ku ukapolo,
watengedwa yense ukapolo.
Tukula maso ako kuti uwone
amene akubwera kuchokera kumpoto.
Kodi nkhosa zimene anakusungitsa zili kuti,
nkhosa zanu zokongola zija?
Kodi udzanena chiyani pamene [Yehova] adzakuyikira
anthu amene unkanena kuti ndi abale ako akukugonjetsa ndi kukulamulira?
Kodi sudzamva zowawa
ngati za mayi pa nthawi yake yochira?
Ndipo ngati udzadzifunsa kuti,
“Kodi zimenezi zandichitikira chifukwa chiyani?”
Ndi chifukwa cha machimo anu ambiri
kuti zovala zanu zingʼambike
ndiponso kuti akuchitireni nkhanza.
Kodi wa dziko la Kusi nʼkusintha khungu lake,
kapena kambuku kusintha mawanga ake?
Inunso amene munazolowera kuchita
zoyipa simungathe kusintha.
“Ine ndidzakumwazani ngati mankhusu
amene amawuluka ndi mphepo ya ku chipululu.
Limeneli ndiye gawo lanu,
chilango chimene ndakukonzerani
chifukwa chondiyiwala Ine
ndi kutumikira milungu yabodza,
akutero Yehova.
Ine ndidzakwinya zovala zanu mpaka ku maso
kuti umaliseche wanu uwonekere.
Ndaona zonyansa zanu: zigololo zanu, kutchetcherera kwanu
ndi ziwerewere zanu,
zochitika pa mapiri ndi mʼminda.
Tsoka iwe Yerusalemu!
Udzakhala wosayeretsedwa
pa zachipembedzo mpaka liti?”
Chilala, Njala, Lupanga
Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:
“Yuda akulira,
mizinda yake ikuvutika;
anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni,
kulira kwa Yerusalemu kwakula.
Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.
Apita ku zitsime
osapezako madzi.
Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi.
Amanyazi ndi othedwa nzeru
adziphimba kumaso.
Popeza pansi pawumiratu
chifukwa kulibe madzi,
alimi ali ndi manyazi
ndipo amphimba nkhope zawo.
Ngakhale mbawala yayikazi
ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo
chifukwa kulibe msipu.
Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu
nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe;
maso awo achita chidima
chifukwa chosowa msipu.”
Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,
koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.
Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu;
ife takuchimwirani.
Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani
ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso,
chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno?
Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,
kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa?
Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu,
ndipo tikudziwika ndi dzina lanu;
musatitaye ife!”
Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:
“Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri;
samatha kudziretsa.
Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire,
ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo
ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usawapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino. Ngakhale asale zakudya, Ine sindidzamva kulira kwawo; ngakhale apereke nsembe zopsereza ndi chopereka cha chakudya, sindidzazilandira. Mʼmalo mwake, ndidzawapha ndi lupanga, njala ndi mliri.”
Koma ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova, aneneri amawawuza anthuwo kuti, sadzaphedwa ndi lupanga kapena kuvutika ndi njala. Koma kuti Inu mudzawapatsa mtendere wokhawokha pamalo pano.”
Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Ndi zabodza kuti aneneriwa akunenera mʼdzina langa. Ine sindinawatume kapena kuwasankha kapenanso kuyankhula nawo. Iwo amakuwuzani zinthu zabodza zomwe amati anaziona mʼmasomphenya, kapena pogwiritsa ntchito mawula achabechabe. Zimene amayankhula ndi zongopeka mʼmutu mwawo. Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti aneneri amenewa akulosera mʼdzina langa pamene Ine sindinawatume. Iwo amati simudzafa pa nkhondo kapena ndi njala mʼdziko muno. Koma tsono ndi iwowo, aneneriwa amene adzafe pa nkhondo kapena ndi njala. Ndipo anthu amene anawaloserawo adzaponyedwa mʼmisewu ya mu Yerusalemu atafa ndi njala ndi lupanga. Sipadzapezeka wowayika mʼmanda popeza iwowo, akazi awo, ana awo aamuna, onse adzakhala atafa. Ine ndidzawagwetsera chilango chowayenera.
“Awuze mawu awa:
“ ‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza
usana ndi usiku;
chifukwa anthu anga okondedwa
apwetekeka kwambiri,
akanthidwa kwambiri.
Ndikapita kuthengo,
ndikuona amene aphedwa ndi lupanga;
ndikapita mu mzinda,
ndikuona amene asakazidwa ndi njala.
Ngakhale aneneri pamodzi
ndi ansembe onse atengedwa.’ ”
Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?
Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni?
Chifukwa chiyani mwatikantha chotere
kuti sitingathenso kuchira?
Ife tinayembekezera mtendere
koma palibe chabwino chomwe chabwera,
tinayembekezera kuchira
koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu
ndiponso kulakwa kwa makolo athu;
ndithu ife tinakuchimwiranidi.
Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;
musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero.
Kumbukirani pangano lanu ndi ife
ndipo musachiphwanye.
Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,
kodi pali mulungu amene angagwetse mvula?
Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu,
popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu
amene mukhoza kuchita zimenezi.
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Ngakhale Mose ndi Samueli akanayima pamaso panga kupempherera anthu awa, Ine sindikanawachitira chisoni. Achotseni ndipo ndisawaonenso! Aleke apite! Ndipo ngati akufunsa iwe kuti, ‘Kodi tipite kuti?’ uwawuze kuti, ‘Yehova akuti,
“ ‘Oyenera kufa adzafa;
oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga;
oyenera kufa ndi njala adzafa ndi njala;
oyenera kupita ku ukapolo adzapita ku ukapolo.’
“Ine ndidzawatumizira mitundu inayi ya zinthu zowononga,” akutero Yehova, “lupanga lowapha, agalu owaluma, mbalame zamumlengalenga ndiponso zirombo zoti ziwadye ndi kuwawononga. Ndidzawasandutsa kukhala chinthu chonyansa kwa anthu a maufumu onse a dziko lapansi chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya mfumu ya Yuda anachita mu Yerusalemu.
“Kodi adzakumvera chisoni ndani, Yerusalemu?
Kodi adzakulira ndani?
Kodi ndani amene adzapatuka kufunsa za moyo wako?
Inu mwandikana Ine,” akutero Yehova.
“Inu mukubwererabe mʼmbuyo.
Choncho Ine ndidzakukanthani.
Ndatopa ndi kukuchitirani chifundo.
Ine ndidzakubalalitsani kukuchotsani mʼmizinda ya mʼdzikomo
monga mmene amachitira ndi mankhusu popeta ndi lichero.
Anthu anga ndinawaliritsa ndi kuwawononga
chifukwa sanasinthe makhalidwe awo oyipa.
Ndinachulukitsa amayi awo amasiye
kupambana mchenga wa kunyanja.
Amayiwo ndinawawonongera ana awo aamuna
dzuwa lili pamutu.
Mwadzidzidzi ndinawagwetsera
kuwawa mtima ndi mantha.
Mayi wa ana asanu ndi awiri wakomoka
ndipo akupuma wefuwefu.
Dzuwa lake lalowa ukanali usana;
anamuchititsa manyazi ndipo wathedwa nzeru.
Otsala ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo
kuti awaphe ndi lupanga,”
akutero Yehova.
Kalanga ine, amayi pakuti munandibereka ine,
munthu amene ndikutsutsana ndi kulimbana ndi anthu pa dziko lonse!
Ine sindinakongoze kapena kukongola kanthu,
komatu aliyense akunditemberera.
Yehova anati,
“Ndithudi, Ine ndidzakulanditsa kuti upeze bwino.
Ndithudi, adani ako adzakupempha pa nthawi ya tsoka
ndi ya mavuto awo.
“Palibe munthu amene angathe kudula chitsulo,
makamaka chitsulo chochokera kumpoto chosakaniza ndi mkuwa.
Anthu ako ndi chuma chako
ndidzazipereka kwa ofunkha popanda malipiro,
chifukwa cha machimo anu onse
a mʼdziko lanu lonse.
Ndidzakusandutsani akapolo a adani anu
mʼdziko limene inu simulidziwa,
chifukwa mkwiyo wanga wayaka ngati moto
umene udzakutenthani.”
Ine ndinati, “Inu Yehova, mumadziwa zonse;
kumbukireni ndi kundisamalira.
Ndilipsireni anthu ondizunza.
Ndilezereni mtima musandilande moyo wanga.
Onani momwe ndi kuvutikira chifukwa cha Inu.
Munandiyankhula ndipo mawu anu ndinawalandira bwino.
Mawu anu anandipatsa chimwemwe ndipo mtima wanga unasangalala.
Paja ine, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,
ndimadziwika ndi dzina lanu.
Sindinakhale nawo mʼgulu la anthu amadyera,
sindinasangalale nawo anthu amenewo.
Ndinakhala ndekha chifukwa choti dzanja lanu linali pa ine
ndipo munadzaza mu mtima mwanga ndi mkwiyo.
Nanga nʼchifukwa chiyani mavuto anga sakutha?
Bwanji chilonda changa sichikupola?
Kodi inu mudzakhala ngati mtsinje wowuma nthawi yachilimwe,
kapena ngati kasupe wopanda madzi?”
Tsono Yehova anandiyankha kuti,
“Ukabwerera kwa Ine, ndidzakulandiranso
ndipo udzakhalanso mtumiki wanga.
Ngati udzayankhula mawu oyenera osati achabechabe,
udzakhalanso mneneri wanga.
Anthu adzabwera kwa iwe
ndipo sipadzafunika kuti iwe upite kwa iwo.
Ndidzakusandutsa ngati khoma lolimba
ngati mkuwa kwa anthu awa.
Adzalimbana nawe
koma sadzakugonjetsa,
pakuti Ine ndili nawe
kukulanditsa ndi kukupulumutsa,”
akutero Yehova.
“Ndidzakupulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa
ndipo ndidzakuwombola kwa anthu ankhanza.”
Tsiku la Masautso
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Usadzakwatire ndi kubereka ana aamuna kapena aakazi malo ano pakuti ana aamuna ndi ana aakazi obadwira mʼdziko muno, komanso amayi awo ndi abambo awo amene anabereka anawo mʼdziko muno, adzafa ndi nthenda zoopsa. Sadzawalira maliro kapena kuyikidwa mʼmanda koma adzakhala ngati ndowe zotayikira pansi. Ena adzaphedwa ku nkhondo ndipo ena adzafa ndi njala. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo zakuthengo.”
Yehova akuti, “Usalowe mʼnyumba ya maliro; usapite kukalira maliro kapena kukapepesa, chifukwa Ine ndawachotsera madalitso anga, chikondi changa ndi chifundo changa.” Akuluakulu ndi angʼonoangʼono omwe adzafa mʼdziko muno. Sadzayikidwa mʼmanda kapena kuliridwa, ndipo palibe amene adzaonetse chisoni podzichekacheka kapena kumeta tsitsi lake chifukwa cha iwo. Palibe amene adzapereka chakudya kutonthoza amene akulira maliro, ngakhale kuti womwalirayo ndi abambo ake kapena amayi ake.
“Ndipo usalowe mʼnyumba mmene muli madyerero, nʼkukhala pansi ndi kudya ndi kumwa nawo. Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Pa nthawi yanu, inu mukuona ndidzathetsa mawu achimwemwe ndi achisangalalo ndiponso mawu a mkwati ndi mkwatibwi pa malo ano.’
“Ukawawuza anthu awa zinthu zonsezi akakufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wanena kuti tsoka lalikulu lotere lidzatigwere? Kodi talakwa chiyani? Kodi tamuchimwira tchimo lotani Yehova Mulungu wathu?’ Pamenepo ukawawuze kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti makolo anu anandisiya Ine,’ akutero Yehova, ‘ndi kutsatira milungu ina, kuyitumikira ndi kuyipembedza. Iwo anandisiya Ine ndipo sanasunge lamulo langa. Komanso inu munachimwa kwambiri kupambana makolo anu. Aliyense wa inu akutsatira zoyipa ndi mtima wake wokanikawo mʼmalo mondimvera Ine. Choncho Ine ndidzakubalalitsani mʼdziko muno ndi kukulowetsani mʼdziko limene inu ndi makolo anu simunalidziwe. Kumeneko mukatumikira milungu ina usana ndi usiku, ndipo sadzakuchitirani chifundo.’ ”
Yehova akuti, “Komabe masiku akubwera pamene anthu polumbira sadzatinso, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto,’ koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku dziko lakumpoto, ndi ku mayiko onse kumene anawabalalitsirako.’ Pakuti ndidzawabwezera ku dziko limene ndinalipereka kwa makolo awo.”
Yehova akuti, “Koma tsopano ndidzayitana adani okhala ngati asodzi ambiri, ndipo adzawagwira ngati nsomba. Izi zitatha adani enanso okhala ngati alenje ambiri, adzawasaka pa phiri lililonse, pa chitunda chilichonse ndiponso mʼmapanga onse a mʼmatanthwe. Maso anga akuona makhalidwe awo onse; sanabisike pamaso panga. Palibe tchimo limene sindikulidziwa. Ndidzawalanga mowirikiza chifukwa cha kuyipa kwawo ndi tchimo lawo. Ndidzatero chifukwa ayipitsa dziko langa ndi mafano awo amene ali ngati mitembo, ndiponso adzaza cholowa changa ndi mafano awo onyansa.”
Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga ndi linga langa,
pothawirapo panga nthawi ya masautso,
anthu a mitundu yonse adzabwera kwa Inu
kuchokera ku mathero onse a dziko lapansi ndipo adzanena kuti,
“Makolo anthu anali ndi milungu yonama,
anali ndi mafano achabechabe amene sanawathandize.
Kodi anthu nʼkudzipangira milungu?
Atati atero ndiye kuti imeneyo ikhala milungu yachabechabe.”
“Choncho Ine ndidzawaphunzitsa,
kokha kano kuti adziwe
za mphamvu yanga ndi za nyonga zanga.
Pamenepo adzadziwa kuti
dzina langa ndi Yehova.
“Tchimo la Yuda lazokotedwa ndi cholembera cha chitsulo,
lalembedwa ndi msonga ya mwala wadayimondi.
Uchimowo walembedwa pa mitima yawo
ndiponso pa nyanga za maguwa awo.
Ngakhale ana awo amakumbukira
maguwa awo ndi zoyimiritsa ngati zifanizo za mulungu wawo Asera,
pa tsinde la mitengo ya masamba ambiri,
pa mapiri aatali mʼdzikomo.
Chuma chanu ndiponso katundu wanu yense
ndidzazipereka kwa ofunkha
kuti zikhale dipo lawo
chifukwa cha machimo
ochitika mʼdziko lonse.
Mudzataya dziko limene ndinakupatsani
kuti likhale cholowa chanu.
Ndidzakusandutsani akapolo otumikira adani anu
mʼdziko limene inu simukulidziwa,
chifukwa mwabutsa mkwiyo wanga ngati moto,
ndipo udzayaka mpaka muyaya.”
Yehova akuti,
“Ndi wotembereredwa munthu amene amadalira munthu mnzake,
amene amatsamira pa munthu mnzake kuti amuthandize
pamene mtima wake wafulatira Yehova.
Munthuyo adzakhala ngati chitsamba mʼchipululu;
iye sadzapeza zabwino.
Adzakhala mʼchipululu mopanda madzi,
mʼdziko lamchere limene munthu sangathe kukhalamo.
“Koma ndi wodala munthu amene amadalira Yehova,
amene amatsamira pa Iye.
Adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi
umene umatambalitsa mizu yake mʼmbali mwa mtsinje.
Mtengowo suopa pamene kukutentha;
masamba ake amakhala obiriwira nthawi zonse.
Suchita mantha pa chaka cha chilala
ndipo sulephera kubereka chipatso.”
Mtima wa munthu ndi wonyenga kupambana zinthu zonse
ndipo kuyipa kwake nʼkosachizika.
Ndani angathe kuwumvetsa?
“Ine Yehova ndimafufuza mtima
ndi kuyesa maganizo,
ndimachitira munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake
ndiponso moyenera ntchito zake.”
Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo
ali ngati nkhwali imene imafungatira mazira amene sinayikire.
Pamene ali pakatikati pa moyo wake, chumacho chidzamuthera,
ndipo potsiriza adzasanduka chitsiru.
Nyumba yathu yopemphereramo ili ngati mpando waufumu waulemerero
wokhazikitsidwa pa phiri lalitali chiyambire.
Inu Yehova, chiyembekezo cha Israeli,
onse amene amakusiyani adzachita manyazi.
Iwo amene amakufulatirani mayina awo adzafafanizika ngati olembedwa pa fumbi
chifukwa anakana Yehova,
kasupe wa madzi amoyo.
Inu Yehova, chiritseni, ndipo ndidzachira;
pulumutseni ndipo ndidzapulumuka,
chifukwa ndinu amene ndimakutamandani.
Anthu akumandinena kuti,
“Mawu a Yehova ali kuti?
Zichitiketu lero kuti tizione!”
Ine sindinakuwumirizeni kuti muwalange.
Mukudziwa kuti ine sindilakalaka tsiku la tsoka.
Zonse zimene ndinayankhula Inu mukuzidziwa.
Musandichititse mantha;
ndinu pothawira panga pa tsiku la mavuto.
Ondizunza anga achite manyazi,
koma musandichititse manyazi;
iwo achite mantha kwambiri,
koma ine mundichotsere manthawo.
Tsiku la mavuto liwafikire;
ndipo muwawononge kotheratu.
Kusunga Tsiku la Sabata
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukayime pa chipata chodzerapo anthu, chimene mafumu a ku Yuda amalowerapo ndi kutulukirapo. Ukayimenso pa zipata zina zonse za Yerusalemu. Ukawawuze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu onse a ku Yuda ndi anthu onse a ku Yuda ndi inu nonse okhala mu Yerusalemu amene mumatulukira pa zipata izi.’ Yehova akuti: samalani kuti pa tsiku la Sabata musanyamule katundu kapena kulowa naye pa zipata za Yerusalemu. Musalowetse katundu mʼnyumba zanu kapena kugwira ntchito pa tsiku la Sabata, koma mulipatule tsiku la Sabatalo, monga ndinalamulira makolo anu. Komatu iwo sanandimvere kapena kulabadira. Ndi mitima yawo yowumayo sanamvere kapena kulandira malangizo anga. Yehova akuti, ‘Muzimvera Ine ndi kuleka kulowetsa kapena kutulutsa katundu pa zipata za mzinda pa tsiku la Sabata. Muzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika posachita ntchito iliyonse pa tsikuli. Mukatero ndiye mafumu anu amene akukhala pa mpando wa Davide adzatulukira pa zipata za mzindawu pamodzi ndi nduna zawo. Iwo pamodzi ndi nduna zawo azidzalowa atakwera magaleta ndi akavalo, akuperekezedwa ndi anthu a ku Yuda ndi amene amakhala mu Yerusalemu, ndipo mu mzinda muno mudzakhala anthu mpaka muyaya. Anthu adzabwera kuchokera ku mizinda ya Yuda ndi ku midzi yozungulira Yerusalemu, kuchokera ku dziko la Benjamini ndi ku mapiri a kumadzulo, kuchokera ku dziko la mapiri ndi ku Negevi. Adzabwera ndi nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi za chakudya, nsembe za lubani ndi zopereka zachiyamiko ku nyumba ya Yehova. Koma ngati simundimvera; mukapanda kusunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika ndi kumanyamula katundu nʼkumalowa naye pa zipata za Yerusalemu pa tsikuli, Ine ndidzabutsa moto pa zipata za Yerusalemu. Moto umenewo udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu ndipo moto wake sudzazima.’ ”
Ku Nyumba ya Wowumba Mbiya
Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Pita ku nyumba ya munthu wowumba mbiya, ndipo kumeneko ndikakuwuza mawu anga.” Choncho ndinatsikira ku nyumba ya wowumba mbiya, ndipo ndinamuona akuwumba mbiya pa mkombero. Tsono amati ngati mbiya imene waumba ikhala yosawumbika bwino ankayiphwanya nʼkuwumbanso ina monga mmene afunira ndi dothi lake lomwe lija.
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Inu Aisraeli, kodi Ine sindingathe kuchita nanu monga amachitira wowumba mbiya?” akutero Yehova. “Inu muli mʼmanja mwanga ngati mtapo mʼmanja mwa wowumba mbiya. Ngati nditalengeza kuti mtundu wina wa anthu kapena ufumu wina ndiwuzula, kuwugwetsa ndi kuwuwononga, ndipo ngati mtundu wa anthu umene ndawuchenjezawo ulapa zoyipa zawo, ndiye kuti Ine ndidzaleka ndipo sindidzabweretsa pa anthuwo mavuto amene ndinakonzekera kuwachitira. Ndipo ngati ndilengeza kuti ndikufuna kumanga ndi kukhazikitsa mtundu wa anthu kapena ufumu. Koma mtunduwo ukachita choyipa pamaso panga nʼkusandimvera, ndiye kuti sindidzawuchitiranso zabwino zimene ndimafuna ndiwuchitire.
“Ndipo tsopano kawawuze anthu a ku Yuda ndi amene akukhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova akuti, Taonani! Ndikukukonzerani mavuto, ndi kuganizira zoti ndikulangeni. Kotero siyani makhalidwe anu oyipa aliyense wa inu, ndipo mukonzenso makhalidwe anu ndi zochita zanu.’ Koma iwo adzayankha kuti, ‘Zimenezo nʼzosathandiza. Ife tidzapitiriza kuchita zomwe takonzekera; aliyense wa ife adzatsatira zoyipa za mtima wake wokanika.’ ”
Yehova akuti,
“Uwafunse anthu a mitundu ina kuti:
Kodi ndani anamvapo zinthu zofanana ndi zimenezi?
Israeli amene anali ngati namwali wanga wachita
chinthu choopsa kwambiri.
Kodi chisanu chimatha pa matanthwe
otsetsereka a phiri la Lebanoni?
Kodi madzi ozizira amitsinje ochokera
ku phiri la Lebanoni adzamphwa?
Komatu anthu anga andiyiwala;
akufukiza lubani kwa mafano achabechabe.
Amapunthwa mʼnjira
zawo zakale.
Amayenda mʼnjira zachidule
ndi kusiya njira zabwino.
Dziko lawo amalisandutsa chipululu,
chinthu chochititsa manyazi nthawi zonse;
onse odutsapo adzadabwa kwambiri
ndipo adzapukusa mitu yawo.
Ngati mphepo yochokera kummawa,
ndidzawabalalitsa pamaso pa adani awo;
ndidzawafulatira osawathandiza
pa tsiku la mavuto awo.”
Anthuwo anati, “Tiyeni, tipangane zoti timuchitire Yeremiya; pakuti ansembe otiphunzitsa malamulo tidzakhala nawobe. Anthu anzeru otilangiza tidzakhala nawo, ndiponso aneneri otilalikira mawu. Choncho tiyeni timupezere chifukwa ndipo tisamvere chilichonse chimene akunena.”
Ndipo ndinapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, ndimvereni;
imvani zimene adani anga akunena za ine!
Kodi chinthu choyipa nʼkukhala dipo la chinthu chabwino?
Komabe iwo andikumbira dzenje.
Kumbukirani kuti ndinadzayima pamaso panu
kudzawapempherera
kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
Choncho langani ana awo ndi njala;
aperekeni kuti aphedwe ndi lupanga.
Akazi awo asanduke opanda ana ndi amasiye;
amuna awo aphedwe ndi mliri,
anyamata awo aphedwe ndi lupanga ku nkhondo.
Kulira kumveke kuchokera mʼnyumba zawo
mutawatumizira gulu lankhondo mwadzidzidzi kuti liwakanthe.
Iwo andikumbira dzenje kuti ndigweremo
ndipo atchera msampha mapazi anga.
Koma Inu Yehova, mukudziwa
ziwembu zawo zonse zofuna kundipha.
Musawakhululukire zolakwa zawo
kapena kufafaniza machimo awo pamaso panu.
Agonjetsedwe pamaso panu;
muwalange muli wokwiya.”
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ukagule mʼphika wadothi kwa munthu wowumba. Utenge akuluakulu ena a anthuwa ndi ansembe ndipo mupite ku Chigwa cha Hinomu chimene chili pafupi ndi pa chipata cha mapale. Pamenepo ukalengeze mawu amene ndikakuwuze. Ukanene kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, inu mafumu a ku Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti: Tamverani! Ine ndibweretsa mavuto pa malo pano mwakuti aliyense amene adzamve adzadzidzimuka. Pakuti anthu andikana Ine ndipo ayipitsa malo ano. Afukiza lubani pa malo ano kwa milungu imene iwo ngakhale makolo awo ngakhalenso mafumu a ku Yuda sanayidziwe. Iwo adzaza malowa ndi magazi a anthu osalakwa. Amanga nsanja zopembedzerapo Baala, kuperekapo ana awo kuti akhale nsembe zopsereza kwa Baala, chinthu chimene Ine sindinalamule kapena kuchiyankhula, ngakhalenso kuchiganizira. Nʼchifukwa chake taonani, masiku akubwera, akutero Yehova, pamene anthu sadzatchulanso malo ano kuti Tofeti kapena Chigwa cha Hinomu, koma Chophera anthu.
“ ‘Pamalo pano ndidzasokoneza maganizo a anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Ndidzachititsa kuti adani awo awaphe ku nkhondo. Ndidzawakanthitsa kwa anthu amene akuwazonda. Mitembo yawo ndidzayipereka kwa mbalame za mlengalenga ndi zirombo za kutchire kuti ikhale chakudya chawo. Mzinda uno ndidzawusakaza ndi kuwusandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyansa. Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo chifukwa cha kuwonongeka kwake. Adani awo adzawuzinga mzindawo kufuna kuwapha motero kuti anthu a mʼkatimo adzafika pomadyana wina ndi mnzake. Adzadya ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.’
“Tsono iwe udzaphwanye mtsukowo anthu amene udzapite nawowo akuona, ndipo ukawawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndidzaphwanya dziko lino ndi mzinda uno ngati momwe wowumba amaphwanyira mbiya yake ndipo sangathe kuyikonzanso. Adzayika anthu akufa ku Tofeti chifukwa padzasowa malo ena owayika. Umu ndi mmene ndidzachitire ndi malo ano pamodzi ndi anthu okhalamo, akutero Yehova. Ndidzasandutsa mzindawu kukhala ngati Tofeti. Nyumba za mu Yerusalemu ndi za mafumu a ku Yuda ndidzazisandutsa ngati za ku Tofeti chifukwa ndi nyumba zimene pa madenga ake ankafukiza lubani kwa zolengedwa zamlengalenga ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’ ”
Kenaka Yeremiya anabwerako ku Tofeti, kumene Yehova anamutuma kuti akanenere, nakayimirira mʼbwalo la Nyumba ya Yehova ndi kuwawuza anthu kuti, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Tamverani! Ine ndidzabweretsa masautso amene ndinanena aja pa mzinda uno ndi pa mizinda yozungulira, chifukwa anthu ake ndi nkhutukumve ndipo sanamvere mawu anga.’ ”
Yeremiya ndi Pasuri
Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi. Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova. Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse. Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo. Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni. Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”
Madandawulo a Yeremiya
Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;
Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.
Anthu akundinyoza tsiku lonse.
Aliyense akundiseka kosalekeza.
Nthawi iliyonse ndikamayankhula,
ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka!
Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka
ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.
Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye
kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,”
mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga,
amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga.
Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa,
koma sindingathe kupirirabe.
Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti,
“Zoopsa ku mbali zonse!
Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!”
Onse amene anali abwenzi anga
akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti,
“Mwina mwake adzanyengedwa;
tidzamugwira
ndi kulipsira pa iye.”
Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu.
Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana.
Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana.
Manyazi awo sadzayiwalika konse.
Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama
ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu.
Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga
popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
Imbirani Yehova!
Mutamandeni Yehova!
Iye amapulumutsa wosauka
mʼmanja mwa anthu oyipa.
Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!
Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga
ndi uthenga woti:
“Kwabadwa mwana wamwamuna!”
Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene
Yehova anayiwononga mopanda chisoni.
Amve mfuwu mmawa,
phokoso la nkhondo masana.
Chifukwa sanandiphere mʼmimba,
kuti amayi anga asanduke manda anga,
mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni
kuti moyo wanga
ukhale wamanyazi wokhawokha?
Mulungu Akana Pempho la Zedekiya
Mfumu Zedekiya inatuma Pasuri mwana wa Malikiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa Yeremiya. Iwo amati akanene kwa Yeremiya mawu akuti, “Tinenere kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni akutithira nkhondo. Mwina mwake Yehova nʼkutichitira zodabwitsa kuti Nebukadinezarayo achoke kwathu kuno.”
Koma Yehova anawuza Yeremiya kuti ayankhe Pasuri ndi Zefaniya kuti, “Kamuwuzeni Zedekiya kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ndikulandeni zida zimene zili mʼmanja mwanu zimene mukugwiritsa ntchito polimbana ndi mfumu ya ku Babuloni ndi ankhondo ake amene akuzingani kunja kwa lingali. Ndipo ndidzasonkhanitsa zidazo mʼkati mwa mzindawu. Ineyo mwini wakene ndi mkono wotambasula ndi dzanja lamphamvu, ndidzachita nanu nkhondo ndili wokwiya, wokalipa ndi waukali. Ndidzakantha amene amakhala mu mzinda muno, anthu pamodzi ndi zirombo, ndipo zidzafa ndi mliri woopsa. Pambuyo pake, ndidzapereka Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi anthu a mu mzinda muno amene adzapulumuke pa nthawi ya mliri, lupanga ndi njala kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi kwa adani awo amene ankafuna kuwapha. Iye adzawapha ndi lupanga. Sadzawachitira chifundo kapena kuwamvera chisoni kapenanso kuwakomera mtima.’
“Yehova anati ndiwawuzenso anthu amenewa kuti asankhe pakati pa moyo ndi imfa. Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzaphedwa ndi lupanga, njala kapena mliri. Koma aliyense amene apite kukadzipereka kwa Ababuloni amene akuzinganiwa adzakhala ndi moyo, adzapulumuka. Ine ndatsimikiza kuchitira mzinda uno choyipa osati chabwino, akutero Yehova. Udzaperekedwa mʼdzanja la mfumu ya ku Babuloni, ndipo iyeyo adzawutentha ndi moto.
“Komanso, uwuze banja laufumu la Yuda kuti, ‘Imva mawu a Yehova; inu a mʼbanja la Davide, Yehova akuti,
“ ‘Weruzani mwachilungamo mmawa uliwonse;
pulumutsani mʼdzanja la wozunza
aliyense amene walandidwa katundu wake,
kuopa kuti ukali wanga ungabuke
ndi kuyaka ngati moto wosazimitsika
chifukwa cha zoyipa zimene mwachita.
Ndidzalimbana nanu,
inu amene mukukhala pamwamba pa chigwa,
inu okhala ngati thanthwe lapachidikha,
akutero Yehova.
Inu amene mumanena kuti, ‘Ndani amene angabwere kudzalimbana nafe?
Ndani amene angathe kulowa mʼmalinga mwathu?’
Ndidzakulangani molingana ndi ntchito zanu,
akutero Yehova.
Ndidzatentha nkhalango zanu;
moto udzapsereza zonse zimene zakuzungulirani.’ ”
Chiweruzo kwa Mafumu Oyipa
Yehova anandiwuza kuti, “Pita ku nyumba ya mfumu ya ku Yuda ndipo ukayiwuze kuti, ‘Imva mawu a Yehova, iwe mfumu ya ku Yuda, amene umakhala pa mpando waufumu wa Davide; iwe, nduna zako pamodzi ndi anthu ako amene amalowera pa zipata izi. Yehova akuti, uziweruza molungama ndi mosakondera. Uzipulumutsa munthu amene walandidwa katundu mʼdzanja la womuzunza. Usazunze kapena kupondereza mlendo, ana amasiye kapena akazi amasiye. Usaphe munthu wosalakwa pa malo pano. Pakuti ngati udzamvera malamulo awa, ndiye kuti mafumu onse okhala pa mpando waufumu wa Davide azidzalowabe pa zipata za nyumba yaufumu ino, atakwera magaleta ndi akavalo, iwowo pamodzi ndi nduna zawo ndi anthu awo. Koma ngati sumvera malamulo awa, akutero Yehova, ndikulumbira pali Ine ndemwe kuti nyumba ino yaufumu idzasanduka bwinja.’ ”
Pakuti zimene Yehova akunena za nyumba yaufumu ya mfumu ya ku Yuda ndi izi:
“Ngakhale iwe uli ngati Giliyadi kwa Ine,
ngati msonga ya phiri la Lebanoni,
komabe ndidzakusandutsa chipululu,
ngati mizinda yopanda anthu.
Ndidzatuma anthu oti adzakuwononge,
munthu aliyense ali ndi zida zake,
ndipo adzadula mikungudza yako yokongola
nadzayiponya pa moto.
“Pamene anthu a mitundu ina adzadutsa pa mzinda umenewu adzafunsana kuti, ‘Chifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere pa mzinda waukuluwu?’ Ndipo yankho lake lidzakhala lakuti, ‘Chifukwa anasiya pangano limene anapangana ndi Yehova Mulungu wawo ndipo anapembedza ndi kutumikira milungu ina.’ ”
Musayilire mfumu Yosiya, musamuyimbire nyimbo womwalirayo;
mʼmalo mwake, mulire kwambiri chifukwa cha Yehowahazi amene wapita ku ukapolo,
chifukwa sadzabwereranso
kapena kuonanso dziko lake lobadwira.
Pakuti zimene Yehova akunena za Yehowahazi mwana wa Yosiya, amene anatenga mpando waufumu wa Yuda mʼmalo mwa abambo ake koma nʼkuwusiya ndi izi: “Iye sadzabwereranso. Iyeyo adzafera ku ukapoloko. Sadzalionanso dziko lino.”
“Tsoka kwa munthu womanga nyumba yake mopanda chilungamo,
womanga zipinda zake zosanja monyenga,
pogwiritsa ntchito abale ake mwathangata,
osawapatsa malipiro a ntchito yawo.
Munthuyo amati, ‘Ndidzadzimangira nyumba yayikulu
ya zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.’
Kotero ndidzapanga mazenera akuluakulu,
ndi kukhomamo matabwa a mkungudza
ndi kukongoletsa ndi makaka ofiira.
“Kodi kukhala ndi nyumba ya mkungudza wambiri
zingachititse iwe kukhala mfumu?
Ganiza za abambo ako. Suja anali ndi zonse zakudya ndi zakumwa.
Abambo ako ankaweruza molungama ndi mosakondera,
ndipo zonse zinkawayendera bwino.
Iye ankateteza anthu osauka ndi osowa,
ndipo zonse zinkamuyendera bwino.
Kodi zimenezi sindiye tanthauzo la kudziwa Ine?”
akutero Yehova.
“Koma maso ako ndi mtima sizili penanso,
koma zili pa phindu lachinyengo,
pa zopha anthu osalakwa
ndi pa kuzunza ndi pakulamulira mwankhanza.”
Nʼchifukwa chake Yehova ponena za Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda akuti,
“Anthu sadzamulira maliro kapena kunena kuti,
‘Kalanga ine, mʼbale wanga! Kalanga ine mlongo wanga!
Anthu ake sadzamulira maliro kuti,
Kalanga ine, mbuye wathu! Taonani ulemerero wake wapita!’
Adzayikidwa ngati bulu,
kuchita kumuguguza ndi kukamutaya
kunja kwa zipata za Yerusalemu.”
“Tsono inu anthu a ku Yerusalemu, pitani ku mapiri a Lebanoni kuti mukalire mofuwula kumeneko,
mawu anu akamveke mpaka ku Basani.
Mulire mofuwula muli ku Abarimu
chifukwa abwenzi ako onse awonongeka.
Ndinakuchenjezani pamene munali pa mtendere.
Koma inu munati, ‘Sindidzamvera.’
Umu ndi mmene mwakhala mukuchitira kuyambira mukali aangʼono.
Simunandimvere Ine.
Mphepo idzakuchotserani abusa anu onse,
ndipo abwenzi anu adzatengedwa ku ukapolo.
Pamenepo mudzachita manyazi ndi kunyozedwa
chifukwa cha zoyipa zanu zonse.
Inu amene mumakhala mʼnyumba ya ku Lebanoni,
amene munamanga nyumba zanu pakati pa mikungudza,
mudzabuwula kwambiri pamene zowawa zidzakugwerani,
zonga za mkazi pa nthawi yake yochira!
“Pali Ine wamoyo, akutero Yehova, ngakhale iwe, Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, ukanakhala ngati mphete ya ku dzanja langa lamanja, ndikanakuvula nʼkukutaya. Ndidzakupereka kwa amene akufuna kukupha, amene iwe umawaopa. Ndidzakupereka kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni ndi anthu ake. Iwe pamodzi ndi amayi ako amene anakubereka ndidzakupititsani ku dziko lachilendo. Ngakhale inu simunabadwire kumeneko, komabe mudzafera komweko. Simudzabwereranso ku dziko limene mudzafuna kubwerera.”
Kodi Yehoyakini wakhala ngati mbiya yonyozeka,
yosweka imene anthu sakuyifunanso?
Kodi nʼchifukwa chake iye pamodzi ndi ana ake,
achotsedwa nʼkutayidwa ku dziko limene iwo sakulidziwa?
Iwe dziko, dziko, dziko,
Imva mawu a Yehova!
Yehova akuti,
“Munthu ameneyu mumutenge ngati wopanda ana,
munthu amene sadzakhala wochita bwino pamoyo wake wonse,
pakuti palibe ndi mmodzi yemwe mwa zidzukulu zake zomwe zidzachita bwino.
Palibe amene adzathe kukhala pa mpando waufumu wa Davide
ndi kulamulira Yuda.”
Nthambi Yolungama
“Tsoka kwa abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa za pabusa panga!” akutero Yehova. Nʼchifukwa chake Yehova, Mulungu wa Israeli, ponena za abusa amene akuweta anthu anga akuti, “Mwabalalitsa ndi kumwaza nkhosa zanga. Komanso simunazisamale bwino. Choncho ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu,” akutero Yehova. “Pambuyo pake Ine mwini wakene ndidzasonkhanitsa nkhosa zanga zotsala, kuzichotsa ku mayiko onse kumene ndinazibalalitsira ndi kuzibweretsanso ku msipu wawo. Kumeneko zidzaswana ndi kuchulukana. Ndidzazipatsa abusa amene adzaziweta, ndipo sizidzaopanso kapena kuchita mantha, ndipo palibe imene idzasochera,” akutero Yehova.
Yehova akuti, “Masiku akubwera,
pamene ndidzaphukitsira Davide Nthambi yowongoka.
Imeneyi ndiye mfumu imene idzalamulira mwanzeru, mwachilungamo ndi mosakondera mʼdziko.
Pa masiku a ulamuliro wake Yuda adzapulumuka
ndipo Israeli adzakhala pamtendere.
Dzina limene adzamutcha ndi ili:
Yehova ndiye Chilungamo Chathu.
Choncho, masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu sadzanenanso polumbira kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa Aisraeli ku Igupto,’ koma adzanena kuti, ‘Pali Yehova wamoyo, amene anatulutsa zidzukulu za Israeli ku dziko lakumpoto ndi ku mayiko konse kumene anawabalalitsira.’ Ndipo iwo adzawabweretsa ku dziko lawolawo.”
Aneneri Onyenga
Kunena za aneneri awa:
Mtima wanga wasweka;
mʼnkhongono mwati zii.
Ndakhala ngati munthu woledzera,
ngati munthu amene wasokonezeka ndi vinyo,
chifukwa cha Yehova
ndi mawu ake opatulika.
Dziko ladzaza ndi anthu achigololo;
lili pansi pa matemberero.
Dziko lasanduka chipululu ndipo msipu wawuma.
Aneneri akuchita zoyipa
ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
“Mneneri ngakhale wansembe onse sapembedza Yehova.
Amachita zoyipa ngakhale mʼnyumba yanga,”
akutero Yehova.
“Nʼchifukwa chake njira zawo zidzakhala zoterera;
adzawapirikitsira ku mdima
ndipo adzagwera kumeneko.
Adzaona zosaona
mʼnthawi ya chilango chawo,”
akutero Yehova.
“Pakati pa aneneri a ku Samariya
ndinaona chonyansa ichi:
Ankanenera mʼdzina la Baala
ndipo anasocheretsa anthu anga, Aisraeli.
Ndipo pakati pa aneneri a ku Yerusalemu
ndaonapo chinthu choopsa kwambiri:
amachita chigololo, amanena bodza
ndipo amalimbitsa mtima anthu ochita zoyipa.
Choncho palibe amene amasiya zoyipa zake.
Kwa Ine anthu onsewa
ali ngati a ku Sodomu ndi Gomora.”
Choncho ponena za aneneriwa Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ndidzawadyetsa zakudya zowawa
ndi kuwamwetsa madzi a ndulu,
chifukwa uchimo umene wafalikira mʼdziko lonse
ndi wochokera kwa aneneri a ku Yerusalemuwa.”
Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Musamvere zimene aneneri amenewa akulosera kwa inu;
zomwe aloserazo nʼzachabechabe.
Iwo akungoyankhula za masomphenya a mʼmitima mwawo basi,
osati zochokera kwa Yehova.
Iwo amapita ndi kumakawuza amene amandinyoza Ine kuti,
‘zinthu zidzakuyenderani bwino.’
Kwa iwo amene amawumirira kutsata zofuna za mitima yawo amakawawuza kuti,
‘palibe choyipa chimene chidzakugwereni.’ ”
Ine ndikuti, “Koma ndani wa iwo amene anakhalapo mu msonkhano wa Yehova?
Ndani anaonapo kapena kumvapo mawu ake?
Ndani mwa iwo analabadirako za mawu ake ndi kuwamvera?
Taonani ukali wa Yehova
uli ngati chimphepo chamkuntho,
inde ngati namondwe.
Ndipo adzakantha mitu ya anthu oyipa.
Mkwiyo wa Yehova sudzaleka
mpaka atachita zonse zimene
anatsimikiza mu mtima mwake.
Mudzazizindikira bwino zimenezi
masiku akubwerawa.”
Yehova anati, “Ine sindinatume aneneri amenewa,
komabe iwo athamanga uku ndi uku kulalikira uthenga wawo;
Ine sindinawayankhule,
komabe iwo ananenera.
Iwo akanakhala pa msonkhano wanga
ndiye kuti akanamayankhula mawu anga kwa anthu anga.
Komanso bwenzi atawachotsa anthu anga mʼnjira zawo zoyipa
kuti aleke machimo awo.”
Yehova akuti, “Kodi ndimakhala Mulungu pokhapokha ndikakhala pafupi,
ndiye sindine Mulungu?
Kodi wina angathe kubisala
Ine osamuona?”
“Kodi Ine sindili ponseponse kumwamba ndi dziko lapansi?”
Akutero Yehova.
“Ndamva zimene aneneri akuyankhula. Iwo amalosera zabodza mʼdzina langa nʼkumati, ‘Ndalota! Ndalota!’ Kodi zabodzazi zidzakhalabe mʼmitima ya aneneriwa mpaka liti? Iwotu amalosera zonyenga za mʼmitima yawo. Aneneriwa amakhulupirira kuti anthu anga adzayiwala mawu anga akamamva za maloto awo amene amayankhulana ngati mmene anachitira makolo awo popembedza Baala. Mneneri amene ali ndi maloto afotokoze malotowo. Koma iye amene ali ndi mawu anga alalikire mawuwo mokhulupirika. Kodi phesi lingafanane ndi chimanga? Kodi suja mawu anga amatentha ngati moto? Suja mawu anga amaphwanya monga ichitira nyundo kuphwanya miyala?” Akutero Yehova.
Yehova akuti, “Nʼchifukwa chake, Ine ndikudana nawo aneneri amene amaberana okhaokha mawu nʼkumati mawuwo ndi a Yehova.” Yehova akuti, “Inde, Ine ndikudana ndi aneneri amene amakonda kuyankhula zabodza nʼkumanena kuti, ‘Amenewa ndi mawu a Yehova.’ ” Yehova akuti, “Ndithudi, Ine ndikudana ndi aneneri a maloto abodzawa. Iwo amafotokoza malotowo nʼkumasocheretsa anthu anga ndi bodza lawo losachita nalo manyazilo, chonsecho Ine sindinawatume kapena kuwalamula. Iwo sathandiza anthuwa ndi pangʼono pomwe,” akutero Yehova.
Uthenga Wabodza ndi Aneneri Abodza
Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Anthu awa, kapena mneneri, kapenanso wansembe, akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga wolemetsa wa Yehova ukuti chiyani?’ uwawuze kuti, ‘Inuyo ndinu katundu wolemetsa Yehova, ndipo adzakutayani.’ Ngati mneneri kapena wansembe kapenanso munthu wina aliyense anena kuti, ‘Uthenga wolemetsa wa Yehova ndi uwu,’ Ine ndidzalanga munthu ameneyo pamodzi ndi banja lake. Koma chimene aliyense wa inu azifunsa kwa mnzake kapena mʼbale wake ndi ichi: ‘Kodi Yehova wayankha chiyani?’ kapena ‘Yehova wayankhula chiyani?’ Koma musanenenso kuti ‘nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ chifukwa mawu a munthu aliyense ndiwo uthenga wa iye mwini, kotero kuti inu mumakhotetsa mawu a Mulungu wamoyo, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wathu. Tsono iwe Yeremiya udzamufunse mneneri kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani?’ kapena, ‘Kodi Yehova wayankhula chiyani?’ Ngati mudzanena kuti, ‘Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova,’ ndiye tsono Yehova akuti, ‘Popeza mwagwiritsa ntchito mawu akuti: Nawu uthenga wolemetsa wa Yehova, mawu amene ndinakuletsani kuti musawatchule, ndiye kuti Ine ndidzakunyamulani ngati katundu nʼkukuponyani kutali. Ndidzakuchotsani pamaso panga, inuyo pamodzi ndi mzinda umene ndinakupatsani inu ndi makolo anu. Ndidzakunyozani mpaka muyaya. Ndidzakuchititsani manyazi osayiwalika.’ ”
Madengu Awiri a Nkhuyu
Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda pamodzi ndi nduna zake, anthu aluso ndi akatswiri a ku Yuda ndi kupita nawo ku Babuloni. Pambuyo pake Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu atayikidwa pa khomo pa Nyumba ya Yehova. Mʼdengu limodzi munali nkhuyu zabwino kwambiri, ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Mʼdengu linalo munali nkhuyu zoyipa kwambiri zosati nʼkudya.
Yehova anandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuona chiyani?”
Ndinayankha kuti, “Ndikuona nkhuyu zabwino kwambiri ndi nkhuyu zoyipa zosati nʼkudya.”
Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Anthu a ku Yuda amene ndinawachotsa ku malo ano nʼkupita nawo ku ukapolo ku dziko la Ababuloni ndikuwafanizira ndi nkhuyu zabwinozi. Ndidzaonetsesa kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzabwera nawonso ku dziko lino. Ndidzawamanga osati kuwapasula; ndidzawadzala osati kuwazula. Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ndine Yehova. Adzakhala anthu anga ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, chifukwa adzabwerera kwa Ine ndi mtima wawo wonse.
“ ‘Koma monga nkhuyu zoyipa zija, zomwe ndi zoyipa kwambiri zosati nʼkudya,’ Yehova akuti, ‘ndi mmene ndidzalangire Zedekiya mfumu ya ku Yuda, nduna zake pamodzi ndi otsala a mu Yerusalemu, kaya adzakhala ali mʼdziko muno kapena mʼdziko la Igupto. Ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa maufumu onse a dziko lapansi, chinthu chonyozeka ndi chopandapake, chinthu chochitidwa chipongwe ndi chotembereredwa kulikonse kumene ndidzawabalalitsira. Ndidzawatumizira nkhondo, njala ndi mliri mpaka atawonongedwa mʼdziko limene ndinawapatsa iwo ndi makolo awo.’ ”
Zaka 70 za Ukapolo
Yehova anayankhula ndi Yeremiya za anthu onse a ku Yuda mʼchaka chachinayi cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, chimene chinali chaka choyamba cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Choncho mneneri Yeremiya anawuza anthu onse a ku Yuda pamodzi ndi onse amene amakhala mu Yerusalemu kuti: Kwa zaka 23, kuyambira chaka cha 13 cha ufumu wa Yosiya mwana wa Amoni mfumu ya ku Yuda mpaka lero lino, Yehova wakhala akundipatsa mauthenga ake ndipo ine ndakhala ndikuyankhula ndi inu kawirikawiri, koma inu simunamvere.
Ndipo ngakhale Yehova kawirikawiri wakhala akukutumizirani atumiki ake onse, aneneri, inuyo simunamvere kapena kutchera khutu. Aneneriwo ankanena kuti, “Ngati aliyense wa inu abwerere, kusiya njira zake zoyipa ndi machitidwe ake oyipa, ndiye kuti mudzakhala mʼdziko limene Yehova anapereka kwa makolo anu kwamuyaya. Musatsatire milungu ina nʼkuyitumikira ndi kuyipembedza. Musapute mkwiyo wanga ndi mafano amene mwapanga ndi manja anu. Mukatero Ine sindidzakuwonongani.
“Koma inu simunandimvere,” akutero Yehova, “ndipo munaputa mkwiyo wanga ndi mafano amene munapanga ndi manja anu. Choncho munadziwononga nokha.”
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Chifukwa simunamvere mawu anga, ndidzayitana mafuko onse akumpoto, pamodzi ndi mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni,” akutero Yehova, “ndipo adzathira nkhondo dziko lino ndi anthu ake pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu ozungulira dzikoli. Ndidzawawononga kwathunthu ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka, mpaka muyaya. Ndidzathetsa mfuwu wachimwemwe ndi wachisangalalo, mawu a mkwati ndi mkwatibwi, phokoso la mphero ndi kuwala kwa nyale. Dziko lonse lidzakhala bwinja ndi chipululu, ndipo mitundu ina idzatumikira mfumu ya ku Babuloni kwa 70.
“Koma zaka 70 zikadzatha, ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi anthu ake, chifukwa cha zolakwa zawo,” akutero Yehova, “ndipo dziko lawo lidzakhala chipululu mpaka muyaya. Ndidzachita zinthu zonse zimene ndinayankhula zotsutsa dzikolo, zonse zimene zalembedwa mʼbuku lino, ndiponso zonse zimene Yeremiya analosera zotsutsa anthu amenewa. Iwo eni adzakhala akapolo a anthu a mitundu yochuluka ndi mafumu amphamvu. Ndidzawabwezera molingana ndi zochita zawo ndi ntchito za manja awo.”
Chikho cha Ukali wa Mulungu
Yehova, Mulungu wa Israeli, anandiwuza kuti, “Tenga chikho ichi chodzaza ndi vinyo wa ukali wanga, ndipo ukamwetse anthu a mitundu yonse kumene ndikukutuma. Akadzamwa adzayamba kudzandira ndi kuchita misala chifukwa cha nkhondo imene ndikuyitumiza pakati pawo.”
Choncho ine ndinatenga chikhocho mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse ya anthu kumene Iye ananditumako: Anandituma ku Yerusalemu ndi ku mizinda ya Yuda, kwa mafumu ake ndi nduna zake kuti ndikawasandutse ngati bwinja ndi chinthu chochititsa mantha ndi chonyozeka ndiponso chotembereredwa, monga mmene alili lero lino. Ananditumanso kwa Farao, mfumu ya ku Igupto, kwa atumiki ake, nduna zake ndi kwa anthu ake onse, ndi kwa anthu ena onse a mitundu yachilendo; mafumu onse a ku Uzi; mafumu onse a Afilisti, a ku Asikeloni, ku Gaza, ku Ekroni ndiponso kwa anthu a ku chigwa chotsala cha Asidodi; Edomu, Mowabu ndi Amoni. Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Turo ndi ku Sidoni; kwa mafumu a kutsidya la nyanja; ku Dedani, ku Tema, ku Buzi ndi kwa onse ometa chamʼmbali. Ananditumanso kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi mafumu onse a anthu achilendo amene amakhala mʼchipululu. Anandituma kwa mafumu onse a ku Zimuri, Elamu ndi Mediya; ndiponso kwa mafumu onse a kumpoto, akufupi ndi kutali omwe, mafumu onse a dziko lapansi. Ndipo potsiriza pake, idzamwenso ndi mfumu Sesaki.
“Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Imwani, ledzerani ndipo musanze, mugwe osadzukanso chifukwa cha nkhondo imene ndikutumiza pakati panu.’ Koma ngati akana kutenga chikhocho mʼdzanja lako ndi kumwa, uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Muyenera kumwa ndithu!’ ” Taonani, tsopano ndiyamba kulanga mzinda uno umene umadziwika ndi dzina langa. Kodi inu muganiza kuti simudzalangidwa? Ayi, simudzapulumuka chifukwa ndikutumiza nkhondo pa onse okhala pa dziko lapansi, akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Tsopano iwe nenera mawu owatsutsa ndipo uwawuze kuti,
“ ‘Yehova adzabangula kumwamba;
mawu ake adzamveka ngati bingu kuchokera ku malo ake opatulika.
Adzabangula mwamphamvu kukalipira dziko lake.
Iye adzafuwula ngati anthu oponda mphesa,
kukalipira onse amene akukhala pa dziko lapansi.
Phokoso lalikulu lidzamveka mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi,
chifukwa Yehova adzazenga mlandu anthu a mitundu yonse;
adzaweruza mtundu wonse wa anthu
ndipo oyipa adzawapha ndi lupanga,’ ”
akutero Yehova.
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani! Mavuto akuti akachoka
pa mtundu wina akukagwa pa mtundu wina;
mphepo ya mkuntho ikuyambira
ku malekezero a dziko.”
Pa tsiku limenelo, onse ophedwa ndi Yehova adzangoti mbwee ponseponse, pa dziko lonse lapansi. Palibe amene adzawalire kapena kusonkhanitsa mitemboyo kuti ikayikidwe mʼmanda, koma idzakhala mbwee ngati ndowe.
Khetsani misozi ndi kufuwula mwamphamvu, abusa inu;
gubudukani pa fumbi, inu atsogoleri a nkhosa.
Pakuti nthawi yanu yophedwa yafika;
mudzagwa ndi kuphwanyika ngati mbiya yabwino kwambiri.
Abusa adzasowa kothawira,
atsogoleri a nkhosa adzasowa malo opulumukira.
Imvani kulira kwa abusa,
atsogoleri a nkhosa akulira,
chifukwa Yehova akuwononga msipu wawo.
Makola awo a nkhosa amene anali pamtendere adzasanduka bwinja
chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
Ngati mkango, Yehova wasiya phanga lake,
pakuti dziko lawo lasanduka chipululu
chifukwa cha nkhondo ya owazunza
ndiponso chifukwa cha mkwiyo woopsa wa Yehova.
Yeremiya Amangidwa
Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda atayamba kulamulira, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Kayime mʼbwalo la Nyumba ya Yehova. Ndipo ukayankhule kwa anthu onse okhala mʼmizinda ya ku Yuda amene amabwera kudzapembedza ku Nyumba ya Yehova. Ukawawuze zonse zomwe ndakulamula; usakasiyeko ndi mawu amodzi omwe. Mwina mwake adzamvera, ndipo aliyense adzatembenuka kuleka njira yake yoyipa. Ndiye ine ndidzaleka osapatsa chilango chimene ndinakonzekera kuti ndiwalange nacho chifukwa cha ntchito zawo zoyipa. Ukawawuze kuti, ‘Yehova akuti: Ngati simundimvera Ine ndi kuleka kutsatira malamulo anga, amene ndakupatsani, ndipo ngati simumvera mawu a atumiki anga, aneneri amene ndakhala ndikukutumizirani, ngakhale kuti simunawamvere, ndiye kuti Ine ndidzasandutsa Nyumba ino kukhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala chinthu chotembereredwa pakati pa mitundu yonse ya pa dziko lapansi.’ ”
Ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akuyankhula mawu amenewa mʼNyumba ya Yehova. Yeremiya atangotsiriza kuwawuza anthu aja zonse zimene Yehova anamulamula kuti ayankhule, ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse anamugwira ndipo anati, “Uyenera kuphedwa! Chifukwa chiyani walosera mʼdzina la Yehova kuti Nyumba ino idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uno udzakhala wopanda anthu ngati chipululu?” Anthu onse anamuzungulira Yeremiya mʼNyumba ya Yehova.
Koma nduna za ku Yuda zitamva zomwe zinachitikazi, zinanyamuka kuchokera ku nyumba yaufumu kupita ku Nyumba ya Yehova, nakakhala pamalo pawo, pa Chipata Chatsopano cha Nyumba ya Yehova. Pamenepo ansembe ndi aneneri anawuza ndunazo pamodzi ndi anthu onse kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa chifukwa amalosera zoyipira mzinda uno. Inu mwadzimvera nokha zimenezi!”
Ndipo Yeremiya anawuza nduna zija ndi anthu onse kuti, “Yehova anandituma kunenera mawu onse amene mwawamva otsutsa Nyumba ino ndi mzinda uno. Tsopano konzani njira zanu ndi zochita zanu ndipo mverani Yehova Mulungu wanu. Mukatero ndiye kuti Yehova adzaleka osakupatsani chilango chimene ankati akupatseni. Kunena za ine, ndili mʼmanja mwanu; mundichite chilichonse chimene mukuganiza kuti ndi chabwino ndi choyenera. Komatu dziwani kuti ngati mundipha, inu pamodzi ndi mzinda uno ndi onse amene amakhala muno, mudzapalamula mlandu wokhetsa magazi a munthu wosalakwa. Ndithudi Yehova anandituma kuti ndidzayankhule mawu onsewa inu mukumva.”
Pamenepo ndunazo pamodzi ndi anthu onse anawuza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthu uyu sayenera kuphedwa! Pakuti wayankhula kwa ife mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.”
Akuluakulu ena a mʼdzikomo anayimirira ndi kuwuza gulu lonse la anthu kuti, “Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
Yerusalemu adzasanduka bwinja,
ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’
Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!”
(Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya. Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto. Komabe Mfumu Yehoyakimu anatuma Elinatani mwana wa Akibori pamodzi ndi anthu ena, ku Igupto. Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).
Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye anateteza Yeremiya, motero sanamupereke kwa anthu kuti amuphe.
Yuda Adzatumikira Nebukadinezara
Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kulamulira, Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako. Tsono utumize uthenga kwa mafumu a Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi Sidoni kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya Yuda. Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti: Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna. Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire. Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.
“ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu. Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”
Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo. Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni? Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”
Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. Musawamvere. Tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mzindawu usandukirenji bwinja? Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni. Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu. Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti, ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ”
Hananiya Atsutsana ndi Yeremiya
Chaka chomwecho mwezi wachisanu wa chaka chachinayi, poyambirira pa ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, amene amachokera ku Gibiyoni, anandiwuza ine mʼNyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akuti, ‘Ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni. Pasanathe zaka ziwiri ndidzabweretsa pa malo ano ziwiya zonse za ku Nyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anazichotsa pa malo pano ndi kupita nazo ku Babuloni. Ndidzabweretsanso pa malo pano Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda pamodzi ndi akapolo ena onse ochokera ku Yuda amene anapita ku Babuloni,’ akutero Yehova, ‘chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya ku Babuloni.’ ”
Pamenepo mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anasonkhana mʼNyumba ya Yehova. Anati, “Ameni! Yehova achitedi zomwezo! Yehova akwaniritse mawu amene waloserawo. Iye abweretsenso pa malo pano ziwiya za mʼNyumba ya Yehova ndi akapolo onse kuchokera ku Babuloni. Komabe, tamvera zimene nditi ndikuwuze iweyo pamodzi ndi anthu onse: Kunali aneneri kalelo, ine ndi iwe tisanabadwe. Iwowa analosera za nkhondo, mavuto ndi mliri kuti zidzagwera mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. Koma mneneri amene amalosera zamtendere adzadziwika kuti ndi woona ndi kuti watumidwa ndi Yehova ngati zimene wanenera zachitikadi.”
Pamenepo mneneri Hananiya anachotsa goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nalithyola, ndipo anawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Umu ndi mmene ndidzathyolere goli la Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonse pasanathe zaka ziwiri.’ ” Zitatero, mneneri Yeremiya anachoka.
Patapita nthawi pangʼono, mneneri Hananiya atathyola goli mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Pita, kawuze mneneri Hananiya kuti, ‘Yehova akuti: Iwe wathyola goli lamtengo, mʼmalo mwake Ine ndidzayika goli lachitsulo. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayika goli lachitsulo mʼkhosi mwa anthu a mitundu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo iwo adzamutumikiradi. Ndipo ndamupatsanso ulamuliro ngakhale pa nyama zakuthengo.’ ”
Ndipo mneneri Yeremiya anawuza mneneri Hananiya kuti, “Tamvera, Hananiya! Iweyo Yehova sanakutume, koma iwe wanyenga anthuwa kuti akhulupirire zabodza. Nʼchifukwa chake Yehova akuti, ‘Ndatsala pangʼono kukuchotsa pa dziko lapansi. Iwe ufa chaka chino chisanathe, chifukwa wakhala ukulalikira zowukira Yehova.’ ”
Mʼmwezi wachisanu ndi chiwiri wa chaka chomwecho, mneneri Hananiya anamwaliradi.
Kalata Yolembera Anthu a ku Ukapolo
Yeremiya anatumiza kalata kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu amene anali ku ukapolo, ndiponso kwa ansembe, aneneri pamodzi ndi anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Zimenezi zinachitika mfumu Yekoniya, amayi a mfumu, nduna za mfumu ndiponso atsogoleri a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, anthu aluso ndi amisiri atatengedwa ku Yerusalemu kupita ku ukapolo. Yeremiya anapatsira kalatayo Eleasa mwana wa Safani ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Zedekiya mfumu ya Yuda anawatumiza kwa Mfumu Nebukadinezara ku Babuloni. Mʼkalatamo analembamo kuti:
Anthu onse amene anatengedwa ukapolo kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Babuloni, Yehova akuwawuza kuti, “Mangani nyumba ndipo muzikhalamo. Limani minda ndipo mudye zipatso zake. Kwatirani ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwasankhire akazi ndipo muwasankhire amuna ana anu aakaziwo, kuti nawonso abale ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko. Chiwerengero chanu chisachepe. Ndiponso muzifunafuna mtendere ndi ubwino wa mzinda umene ndinakupirikitsirani ku ukapoloko. Muzipempherera mzindawo kwa Yehova, kuti zikuyendereni bwino.” Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, “Musalole kuti aneneri ndi owombeza amene ali pakati panu akunyengeni. Musamvere maloto awo. Iwo akunenera zabodza kwa inu mʼdzina langa ngakhale Ine sindinawatume,” akutero Yehova.
Yehova akuti, “Zaka 70 za ku Babuloni zikadzatha, ndidzabwera kudzakuchitirani zabwino zonse zimene ndinakulonjezani zija, ndipo ndidzakubwezerani ku malo ano. Pakuti Ine ndikudziwa zimene ndinakukonzerani,” akutero Yehova, “ndimalingalira zabwino zokhazokha za inu osati zoyipa, ayi. Ndimalingalira zinthu zokupatsani chiyembekezo chenicheni pa za mʼtsogolo. Nthawi imeneyo mudzandiyitana, ndi kunditama mopemba ndipo ndidzakumverani. Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza. Mukadzandifuna ndi mtima wanu wonse mudzandipezadi,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubwezerani zabwino zanu. Ndidzakusonkhanitsani kuchokera ku mayiko onse ndi kumalo konse kumene munali,” akutero Yehova, “ndipo ndidzakubweretsani kumalo kumene munali ndisanakuchotseni kukupititsani ku ukapolo.”
Inu mumati, “Yehova watiwutsira aneneri athu ku Babuloni,” koma zimene Yehova akunena za mfumu imene ikukhala pa mpando waufumu wa Davide pamodzi ndi anthu onse amene anatsala mu mzinda muno, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo ndi izi, Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ndidzawapha ndi nkhondo, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa ngati nkhuyu zowola kwambiri, zosati nʼkudya. Ndidzawalondola ndi lupanga, njala ndi mliri ndipo ndidzawasandutsa chinthu chonyansa kwa anthu amayiko onse a pa dziko lapansi. Adzakhala otembereredwa, ochititsa mantha, onyozeka ndiponso ochitidwa chipongwe pakati pa anthu a mitundu yonse kumene ndawapirikitsirako. Zidzatero chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinkawatumizira kudzera mwa atumiki anga, aneneri. Ngakhale inu amene muli ku ukapolo simunamverenso,” akutero Yehova.
Choncho, imvani mawu a Yehova, inu akapolo nonse amene ndinakuchotsani mu Yerusalemu ndi kukupititsani ku Babuloni. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti zokhudza Ahabu mwana wa Kolaya ndi Zedekiya mwana wa Maseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa: “Taonani ndidzawapereka kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzawapha inu mukupenya. Chifukwa cha anthu awiriwo, akapolo onse ochokera ku Yuda amene ali ku Babuloni adzagwiritsa ntchito mawu awa potemberera: ‘Yehova achite nawe monga mmene anachitira ndi Zedekiya ndi Ahabu, amene mfumu ya ku Babuloni inawatentha.’ Pakuti anthu amenewa achita zoyipa kwambiri mu Israeli; achita chigololo ndi akazi a eni ake ndipo mʼdzina langa ankayankhula zabodza zimene sindinawawuze kuti atero. Ine ndikuzidziwa ndipo ndine mboni ya zimenezi,” akutero Yehova.
Kalata ya Semaya
Ukamuwuze Semaya wa ku Nehelamu kuti, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Iwe unatumiza kalata mʼdzina lako kwa anthu onse a mu Yerusalemu, kwa Zefaniya mwana wa wansembe Maseya, ndi kwa ansembe onse. Unalemba mu kalatayo kuti, ‘Yehova wakusankha kukhala wansembe mʼmalo mwa Yehoyada kuti ukhale wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Yehova. Munthu aliyense wamisala amene akudziyesa kuti ndi mneneri uzimuponya mʼndende ndi kumuveka goli lachitsulo. Nanga tsono chifukwa chiyani simunamuchitire zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu? Yeremiyayo watitumizira uthenga uwu kuno ku Babuloni: Ukapolo wanu ukhala wa nthawi yayitali. Choncho mangani nyumba ndipo muzikhalamo; limani minda ndipo mudye zipatso zake.’ ”
Koma wansembe Zefaniya anayiwerenga kalatayo pamaso pa mneneri Yeremiya. Ndipo Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Tumiza uthenga uwu kwa akapolo onse: ‘Yehova akuti zokhudza Semaya wa ku Nehelamu: Semaya wakuloserani, ngakhale kuti Ine sindinamutume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira bodza. Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova.
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndakuwuza. Nthawi ikubwera pamene ndidzachotse anthu anga, Israeli ndi Yuda kuchokera ku ukapolo ndi kuwabwezera dziko limene ndinapatsa makolo awo,’ akutero Yehova.”
Nawa mawu amene Yehova anayankhula ndi anthu a ku Israeli ndi Yuda: “Yehova akuti:
“Ndamva kulira chifukwa cha nkhawa,
ndamva kulira kwa mantha popeza palibe mtendere.
Tsono khalani pansi ndi kudzifunsa kuti:
Kodi munthu wamwamuna angathe kubereka mwana?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona munthu aliyense wamwamuna
atagwira manja ake pa mimba pake ngati mayi pa nthawi yake yochira?
Chifukwa chiyani nkhope iliyonse ili yakugwa?
Mayo ine! Tsiku limeneli ndi lalikulu kwambiri!
Sipadzakhala lina lofanana nalo.
Idzakhala nthawi ya masautso kwa Yakobo,
koma adzapulumuka ku masautsowo.”
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Pa tsiku limenelo,
ndidzathyola goli la ukapolo mʼkhosi mwawo
ndipo ndidzadula zingwe zowamanga;
Aisraeli sadzakhalanso akapolo a alendo.
Mʼmalo mwake, adzatumikira Yehova Mulungu wawo
ndiponso Davide mfumu yawo,
amene ndidzawasankhira.
“ ‘Tsono usachite mantha, iwe mtumiki wanga Yakobo;
usade nkhawa, iwe Israeli,’
akutero Yehova.
‘Ndithu ndidzakupulumutsa kuchokera ku dziko lakutali,
zidzukulu zako kuchokera ku dziko la ukapolo wawo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala modekha pa mtendere,
ndipo palibe amene adzamuchititsa mantha.
Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani,’
akutero Yehova.
‘Ngakhale ndidzawononga kotheratu mitundu yonse ya anthu
kumene ndinakubalalitsirani,
koma inu sindidzakuwonongani kotheratu.
Sindidzakulekani kuti mukhale osalangidwa.
Koma ndidzakulangani mwachilungamo.’ ”
Yehova akuti,
“Chilonda chanu nʼchosachizika,
bala lanu ndi lonyeka.
Palibe amene angathe kukutetezani pa mlandu wanu,
palibe chiyembekezo choti inu nʼkuchira,
palibe mankhwala ochiritsa inu.
Abwenzi anu onse akuyiwalani;
sasamalanso za inu.
Ndakukanthani ngati mmene mdani akanachitira.
Ndipo ndakulangani mwa nkhanza,
chifukwa machimo anu ndi ambiri,
ndipo kulakwa kwanu ndi kwakukulu.
Chifukwa chiyani mukulira nacho chilonda chanu?
Bala lanu silingapole ayi.
Ine ndakuchitani zimenezi chifukwa machimo anu ndi ambiri
ndipo kulakwa kwanu nʼkwakukulu.
“Tsono onse amene anakuwonongani, nawonso adzawonongedwa;
adani anu onse adzapita ku ukapolo.
Iwo amene anafunkha zinthu zanu, zinthu zawo zidzafunkhidwanso;
onse amene anakusakazani nawonso adzasakazidwa.
Ndidzachiza matenda anu
ndi kupoletsa zilonda zanu,
akutero Yehova,
‘chifukwa mukutchedwa anthu otayika.
Amati, ndi anthu a ku Ziyoni awa amene alibe wowasamala.’ ”
Yehova akuti,
“Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo
ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;
mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,
nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova
ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo.
Ndidzawachulukitsa,
ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika;
ndidzawapatsa ulemerero,
ndipo sadzanyozedwanso.
Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale,
ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga;
ndidzalanga onse owazunza.
Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo.
Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo.
Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira.
Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane
popanda kuyitanidwa?”
akutero Yehova.
“Choncho inu mudzakhala anthu anga,
ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”
Taonani ukali wa Yehova wowomba
ngati mphepo ya mkuntho.
Mphepo ya namondwe
ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.
Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka
mpaka atakwaniritsa zolinga
za mu mtima mwake.
Mudzamvetsa zimenezi
masiku akubwerawo.
“Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “Ndidzakhala Mulungu wa mafuko onse a Israeli, ndipo iwo adzakhala anthu anga.”
Yehova akuti,
“Anthu amene anapulumuka ku nkhondo
ndinawakomera mtima mʼchipululu;
pamene Aisraeli ankafuna kupumula.”
Ine ndinawaonekera ndili chapatali ndipo ndinati,
“Ine ndakukondani ndi chikondi chopanda malire.
Nʼchifukwa chake ndipitiriza kukukondani.
Ndidzakusamaliraninso, inu anthu a Israeli;
mudzasangalala poyimba tizitoliro tanu,
ndipo mudzapita kukavina nawo
anthu ovina mwachimwemwe.
Mudzalimanso minda ya mpesa
pa mapiri a Samariya;
alimi adzadzala mphesa
ndipo adzadya zipatso zake.
Lidzafika tsiku pamene alonda adzafuwula
pa mapiri a Efereimu nati,
‘Tiyeni tipite ku Ziyoni,
kwa Yehova Mulungu wathu.’ ”
Yehova akuti,
“Imbani mosangalala chifukwa cha Yakobo,
fuwulani chifukwa cha mtundu wopambana mitundu yonse.
Matamando anu amveke, ndipo munene kuti,
‘Yehova wapulumutsa anthu ake
otsala a Israeli.’
Taonani, ndidzabwera nawo kuchokera ku dziko la kumpoto,
ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Anthu osaona, olumala, amayi oyembekezera
ndi amene ali pa nthawi yawo yochira adzabwera nawo pamodzi.
Chidzakhala chikhamu cha anthu obwerera kuno.
Adzabwera akulira;
koma Ine ndikuwatonthoza mtima, ndidzawaperekeza.
Ndidzawatsogolera ku mitsinje yamadzi
mʼnjira yosalala mmene sadzapunthwamo.
Chifukwa ndine abambo ake a Israeli,
ndipo Efereimu ndi mwana wanga woyamba.
“Imvani mawu a Yehova inu anthu a mitundu ina;
lalikirani mawuwa kwa anthu a mayiko akutali a mʼmbali mwa nyanja;
‘Iye amene anabalalitsa Israeli adzawasonkhanitsanso
ndipo adzayangʼanira nkhosa zake ngati mʼbusa.’
Pakuti Yehova wawombola fuko la Yakobo
anawapulumutsa mʼdzanja la anthu owaposa mphamvu.
Anthuwo adzabwera akuyimba mofuwula pa mapiri a Ziyoni;
adzasangalala ndi zinthu zabwino zochokera kwa Yehova.
Zinthu zabwinozo ndi izi: tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta,
ana ankhosa ndi ana angʼombe.
Iwo adzakhala ngati munda wothiriridwa bwino,
ndipo sadzamvanso chisoni.
Pamenepo anamwali adzavina ndi kusangalala.
Anyamata ndi okalamba nawonso adzasangalala.
Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo;
ndidzawasangalatsa nʼkuchotsa chisoni chawo.
Ansembe ndidzawadyetsa chakudya chabwino,
ndipo anthu anga adzakhuta ndi zabwino zanga,”
akutero Yehova.
Yehova akuti,
“Kulira kukumveka ku Rama,
kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake.
Sakutonthozeka
chifukwa ana akewo palibe.”
Yehova akuti,
“Leka kulira
ndi kukhetsa misozi
pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,”
akutero Yehova.
“Iwo adzabwerako ku dziko la adani.
Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”
akutero Yehova.
“Ana ako adzabwerera ku dziko lawo.
“Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,
‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva.
Koma inu mwatiphunzitsa kumvera.
Mutibweze kuti tithe kubwerera,
chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.
Popeza tatembenuka mtima,
ndiye tikumva chisoni;
popeza tazindikira
ndiye tikudziguguda pachifukwa.
Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa
chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’
Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,
mwana amene Ine ndimakondwera naye?
Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,
ndimamukumbukirabe.
Kotero mtima wanga ukumufunabe;
ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”
akutero Yehova.
“Muyike zizindikiro za mu msewu;
muyimike zikwangwani.
Yangʼanitsitsani msewuwo,
njira imene mukuyendamo.
Bwerera, iwe namwali wa Israeli,
bwerera ku mizinda yako ija.
Udzakhala jenkha mpaka liti,
iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?
Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’ Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa. Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”
Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.
“Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzachulukitsa anthu pamodzi ndi ziweto mʼdziko la Israeli ndi la Yuda. Monga momwe ndinasamalira powazula, powagwetsa, powagumula, powawononga ndi powachita zoyipa, momwemonso ndidzasamala powamanga ndi powadzala” akutero Yehova. “Mʼmasiku amenewo anthu sadzanenanso kuti,
“Makolo adya mphesa zosapsa,
koma mano a ana ndiye achita dziru.
Mʼmalo wake, munthu aliyense adzafa chifukwa cha tchimo lake. Iye amene adzadye mphesa zosapsazo ndiye amene mano ake adzachite dziru.”
“Masiku akubwera,” akutero Yehova,
“pamene ndidzachita pangano latsopano
ndi Aisraeli
ndiponso nyumba ya Yuda.
Silidzakhala ngati pangano
limene ndinachita ndi makolo awo
pamene ndinawagwira padzanja
nʼkuwatulutsa ku Igupto;
chifukwa anaphwanya pangano langa,
ngakhale ndinali mwamuna wawo,”
akutero Yehova.
“Ili ndi pangano limene ndidzachita ndi Aisraeli
atapita masiku amenewo,” akutero Yehova.
“Ndidzayika lamulo langa mʼmitima mwawo
ndi kulilemba mʼmaganizo mwawo.
Ine ndidzakhala Mulungu wawo
ndipo iwo adzakhala anthu anga.
Sipadzafunikanso kuti wina aphunzitse mnzake,
kapena munthu wina kuphunzitsa mʼbale wake, kunena kuti, ‘Mudziwe Yehova,’
chifukwa onse adzandidziwa Ine,
kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”
akutero Yehova.
“Ndidzawakhululukira zoyipa zawo
ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.”
Yehova akuti,
Iye amene amakhazikitsa dzuwa
kuti liziwala masana,
amene amalamula kuti mwezi ndi nyenyezi
ziziwala usiku,
amene amavundula nyanja
kuti mafunde akokome,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
Ngati zimenezi zilekeka pamaso panga, akutero Yehova, pamenepo padzakhala pamathero a fuko la Israeli pamaso panga.
Yehova akuti,
“Ndidzataya fuko la Israeli chifukwa cha machimo awo.
Ngati patapezeka munthu
amene angathe kupima zakuthambo
nʼkufufuza maziko a dziko lapansi.”
“Taonani masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene mzinda wa Yehova udzamangidwanso kuyambira ku Nsanja ya Hananeli mpaka ku Chipata cha Ngodya. Malire ake adzayambira pamenepo kupita ku phiri la Garebu, nʼkudzakhota kuloza ku Gowa. Chigwa chonse mʼmene amatayiramo mitembo ndi phulusa, ndiponso minda yonse kuyambira ku Chigwa cha Kidroni mpaka ku ngodya ya Chipata cha Akavalo mbali ya kummawa, adzakhala malo opatulika a Yehova. Mzindawu sadzawuzulanso kapena kuwuwononga.”
Yeremiya Agula Munda
Yehova anayankhula ndi Yeremiya mʼchaka chakhumi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, chimene chinalinso chaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara. Pa nthawi imeneyi nʼkuti ankhondo a mfumu ya ku Babuloni atazinga Yerusalemu, ndipo mneneri Yeremiya ndiye anamutsekera mʼbwalo la alonda mʼnyumba yaufumu ya ku Yuda.
Tsono Zedekiya mfumu ya Yuda nʼkuti itamutsekera mʼmenemo, ndipo inati, “Nʼchifukwa chiyani ukulosera motero? Iwe ukunena kuti, ‘Yehova akuti: Ndidzapereka mzinda uno kwa mfumu ya ku Babuloni, ndipo idzawulanda. Zedekiya mfumu ya Yuda sidzapulumuka mʼmanja mwa Ababuloni, koma idzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni. Adzayankhula naye ndi kuonana naye maso ndi maso. Zedekiya adzatengedwa kupita naye ku Babuloni, kumene adzakhale mpaka nditamukhawulitsa, akutero Yehova. Ngakhale iye adzamenyane ndi Babuloni, koma sadzapambana.’ ”
Yeremiya anati, “Yehova wandiwuza kuti: Taonani, Hanameli mwana wa Salumu, amalume ako akubwera ndipo adzakuwuza kuti, ‘Gula munda wanga wa ku Anatoti, chifukwa iwe ndiwe mʼbale wanga ndipo ndiwe woyenera kuwuwombola.’ ”
Ndipo monga momwe Yehova ananenera, Hanameli, msuweni wanga anabweradi ku bwalo la alonda ndipo anati, “Gula munda wanga wa ku Anatoti mʼdziko la Benjamini. Popeza ndiwe woyenera kuwugula ndi kukhala wako, gula munda umenewu kuti ukhale wako.”
“Ine ndinadziwa kuti amenewa anali mawu a Yehova aja; choncho ndinagula munda wa ku Anatoti kwa Hanameli msuweni wanga, ndipo ndinamupatsa masekeli asiliva 17. Ndinasayina panganolo ndikulimata pamaso pa mboni, kenaka ndinayeza ndalama zasilivazo pa sikelo.” Pambuyo pake ndinatenga makalata anga a pangano, imodzi yomatidwa mʼmene munali malamulo onse a panganolo ndi ina yosamatidwa. Ndinapereka makalatawo kwa Baruki mwana wa Neriya, mdzukulu wa Maseya pamaso pa Hanameli msuweni wanga, pamaso pa mboni zimene zinasayina panganoli ndiponso pamaso pa Ayuda onse okhala mʼbwalo la alonda.
“Ndinamulangiza Baruki pamaso pa onsewo kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Tenga makalata awa a umboni wapangano, iyi yokhala ndi chizindikiro ndi yopanda chizindikiro, uwasunge mʼmbiya kuti akhale nthawi yayitali. Pakuti Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Anthu adzagulanso nyumba, minda ndi mitengo yamphesa mʼdziko lino.’ ”
Nditamupatsa makalata a panganowa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova:
“Aa, inu Ambuye Yehova, munalenga dziko lakumwamba ndi dziko lapansi. Munazilenga ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo palibe chokulakani. Mumaonetsa chikondi chanu kwa anthu osawerengeka koma mumalanga ana chifukwa cha machimo a makolo awo. Inu ndinu Mulungu Wamkulu ndi Wamphamvu. Dzina lanu ndinu Yehova Wamphamvuzonse. Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu. Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita. Mumapereka mphotho kwa munthu aliyense molingana ndi makhalidwe ake ndi ntchito zake. Inu munachita zizindikiro zozizwitsa ku Igupto, ndipo mwakhala mukuzichita mpaka lero, pakati pa Aisraeli ndiponso pakati pa anthu onse. Choncho mwadzitchukitsa mpaka lero lino. Munatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu pochita zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa zimene zinaopseza adani anu. Munawapatsa dziko lino limene munalonjeza mwalumbiro kulipereka kwa makolo awo, dziko loyenda mkaka ndi uchi. Iwo analowa nʼkulitenga kukhala lawo, koma sanamvere Inu kapena kutsatira lamulo lanu; ndipo sanachite zomwe munawalamula. Choncho inu mwawagwetsera masautso onsewa.”
“Onani momwe adani azingira ndi mitumbira yankhondo mzindawu kuti awulande ndipo akuwuthira nkhondo. Chifukwa cha lupanga, njala ndi mliri. Mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni anthu atafowoka ndi nkhondo, njala ndi mliri. Zimene munkanena zija zachitikadi monga mukuzionera tsopano. Ngakhale mzindawu udzaperekedwa kwa Ababuloni, komabe Inu Ambuye Yehova, munandiwuza kuti, ‘Gula munda ndi siliva ndipo upereke ndalamazo pali mboni.’ ”
Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Taonani, Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse. Kodi chilipo chinthu choti Ine nʼkundikanika? Nʼchifukwa chake ine Yehova ndikuti: Ndidzawupereka mzinda uno kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulanda. Ndipo Ababuloni amene akuwuthira nkhondo mzinda uno adzalowa ndi kuwutentha; adzatentha ndi kugwetsa nyumba zimene pa denga pake anthu ankandipsetsa mtima pofukiza lubani kwa Baala ndi popereka chopereka cha chakumwa kwa milungu ina.
“Aisraeli ndi Ayuda akhala akuchita zoyipa zokhazokha pamaso panga kuyambira ubwana wawo. Kunena zoona Aisraeli akumandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa, akutero Yehova. Kuyambira tsiku limene mzindawu unamangidwa mpaka lero, wakhala ukuwutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga. Nʼchifukwa chake ndiyenera kuwuchotsa pamaso panga. Aisraeli ndi Ayuda, anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu, mafumu awo, nduna zawo, ansembe ndi aneneri awo anandikwiyitsa ndi ntchito zawo zoyipa. Anandifulatira ndipo ngakhale ndinakhala ndikuwaphunzitsa kawirikawiri, sanamve kapena kuphunzirapo kanthu. Iwo anayika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa ndipo anayipitsa. Anamanga malo opembedzerapo Baala mʼChigwa cha Hinomu kuti aziperekapo ana awo aamuna ndi aakazi ngati nsembe kwa Moleki. Ine sindinawalamulire kutero, ndipo sindinaganizepo nʼkomwe kuti iwo angachite chinthu chonyansa chotero, ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda.
“Anthu ponena za mzindawu akuti udzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni mwa nkhondo, njala ndi mliri, koma Yehova Mulungu wa Israeli akuti, Ine ndidzawasonkhanitsadi anthuwa kuchokera ku mayiko onse kumene ndinawapirikitsira ndili wokwiya ndi waukali kwambiri. Ndidzabwera nawo ku malo ano ndipo ndidzawalola kukhala mwamtendere. Iwo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. Ndidzawapatsa mtima umodzi ndi khalidwe limodzi kotero kuti azidzandiopa nthawi zonse ndipo iwo pamodzi ndi zidzukulu zawo zinthu zidzawayendera bwino. Ndidzachita nawo pangano losatha: sindidzaleka kuwachitira zabwino, ndipo ndidzawapatsa mtima woti azidzandiopa, kuti asadzandisiyenso. Ndidzakondwera powachitira zabwino, ndipo ndidzawakhazikitsa ndithu mʼdziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
“Yehova akuti: Monga momwe ndinagwetsera masautso aakulu onsewa pa anthuwa, momwemonso ndidzawapatsa zinthu zonse zabwino zimene ndinawalonjeza. Adzagulanso minda mʼdziko muno, limene inu mukuti, ‘Ndi dziko losiyidwa, lopanda anthu kapena nyama, pakuti linaperekedwa kwa Ababuloni.’ Adzagula minda ndi ndalama zasiliva, ndipo achita pangano, ndi kumata pamaso pa mboni. Izi zidzachitika mʼdziko la Benjamini, ku malo ozungulira Yerusalemu, mʼmizinda ya Yuda, mʼmizinda ya ku mapiri, mʼmizinda ya kuchigwa ndi yakummwera ku Negevi. Zoona, ndidzabwezera ufulu wawo, akutero Yehova.”
Lonjezo la Kubwezeretsedwa
Yeremiya akanali mʼndende mʼbwalo la alonda, Yehova anayankhula nayenso kachiwiri nati: “Yehova amene analenga dziko lapansi, kuliwumba ndi kulikhazikitsa; amene dzina lake ndi Yehova, akuti, ‘Unditame mopemba ndipo ndidzakuyankha. Ndidzakuwuza zinsinsi zazikulu zimene suzidziwa.’ Yehova Mulungu wa Israeli akunenapo pa za nyumba za mu mzinda muno ndiponso pa za nyumba za mafumu a Yuda. Zidzagwetsedwa, ndipo palibe chifukwa cholimbana ndi mitumbira ya nkhondo ya Ababuloni. Ababuloni akubwera kudzawuthira nkhondo mzindawu ndipo nyumba zake zidzadzaza ndi mitembo ya anthu amene ndidzawapha mokwiya ndi mwaukali. Ndawufulatira mzinda uno chifukwa cha zoyipa zake zonse.
“ ‘Pambuyo pake mzindawu ndidzawupatsanso moyo ndi kuwuchiritsa; ndidzachiritsa anthu anga ndi kuwapatsa chitetezo ndi mtendere weniweni. Ndidzawakhazikanso Ayuda ndi Aisraeli ku dziko lawo, ndipo ndidzawabwezera monga mmene analili poyamba. Ndidzawayeretsa pochotsa zoyipa zonse zimene anandichitira, ndiponso ndidzawakhululukira machimo onse amene anachita pondiwukira. Mzinda wa Yerusalemu udzandipatsa chimwemwe, chiyamiko ndi ulemerero. Anthu a mitundu yonse adzanditamanda akadzamva za zabwino zonse zimene ndawuchitira mzindawu. Iwo adzachita mantha ndi kunjenjemera poona madalitso ochuluka ndi mtendere zimene ndapereka kwa mzinda umenewu.’
“Yehova akuti, ‘Inu mumanena za malo ano kuti ndi bwinja,’ malo opandamo anthu kapena nyama. Komatu mizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu mʼmene tsopano muli zii mudzamvekanso mfuwu wachimwemwe ndi mawu achisangalalo, mawu a mkwatibwi ndi mkwati. Mʼnyumba ya Mulungu mudzamvekanso nyimbo za anthu amene akudzapereka nsembe zothokoza Yehova. Azidzati,
“Yamikani Yehova Wamphamvuzonse,
popeza Iye ndi wabwino;
pakuti chifundo chake nʼchamuyaya.”
Pakuti ndidzabwezeretsa zinthu zabwino za dziko lino monga zinalili poyamba, akutero Yehova.
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Malo ano, a chipululu ndi wopanda anthu kapena nyama, mʼmizinda yake yonse mudzakhala msipu umene abusa adzadyetserako nkhosa zawo. Ku mizinda ya kumapiri, ya kuchigwa, ya ku Negevi, ya ku dera la Benjamini, ku dziko lozungulira Yerusalemu, ndi ku mizinda ya Yuda, nkhosa zidzadutsanso pamaso pa munthu woziwerenga,’ akutero Yehova.
“ ‘Taonani masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene ndidzachitadi zokoma zimene ndinalonjeza Aisraeli ndi nyumba ya Yuda.
“ ‘Mʼmasiku amenewo ndi pa nthawi imeneyo
ndidzaphukitsa Nthambi yolungama kuchokera ku banja la Davide;
munthuyo adzachita zolungama ndi zabwino mʼdziko.
Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumuka
ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.
Dzina limene mzindawu udzadziwike nalo ndi ili:
Yehova Chilungamo Chathu.’
Yehova akunena kuti, ‘Davide sadzasowa mdzukulu wolowa mʼmalo mwake pa mpando waufumu wa Israeli, ngakhale ansembe, amene ndi Alevi, sadzasowanso munthu woyima pamaso panga nthawi zonse wopereka nsembe zopsereza, nsembe zaufa ndi nsembe zina.’ ”
Yehova anawuza Yeremiya kuti: Mawu anga ndi awa. Ine ndinachita pangano ndi usana ndi usiku kuti zizibwera pa nthawi yake. Pangano limeneli inu simungaliphwanye. Ndinachitanso pangano ndi Davide, mtumiki wanga kuti nthawi zonse adzakhala ndi mdzukulu wodzakhala pa mpando wake waufumu. Ndinachitanso pangano ndi Alevi kuti iwonso adzanditumikira nthawi zonse. Mapangano amenewa sadzaphwanyidwa nthawi zonse. Ndidzachulukitsa ngati nyenyezi zamlengalenga ndiponso ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja zidzukulu za mtumiki wanga Davide ndiponso za Alevi amene amanditumikira Ine.
Yehova anafunsa Yeremiya kuti, “Kodi sunamve mmene anthu ena akumanenera kuti, ‘Yehova wakana maufumu awiriwa amene Iye anawasankha.’ Kotero anthuwo akunyoza anthu anga ndipo sakuwayesanso mtundu wa anthu. ‘Koma Ine Yehova ndinachita pangano ndi usana ndi usiku. Ndinakhazikitsanso malamulo oyendetsa dziko lakumwamba ndi dziko lapansi, monga ndachita zimenezi motsimikiza, choncho ndidzasunga pangano limene ndinachita ndi zidzukulu za Yakobo ndi Davide mtumiki wanga. Ndidzasankha mmodzi mwa ana a Davide kuti alamulire zidzukulu za Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Komatu ndidzawamvera chifundo ndi kuwakhazikanso pabwino.’ ”
Chenjezo kwa Zedekiya
Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi gulu lake lonse lankhondo, pamodzi ndi maufumu onse a pa dziko lapansi amene ankawalamulira ndiponso anthu a mitundu yonse ankathira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda yonse yozungulira Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Yehova, Mulungu wa Israeli akuti: Pita kwa Zedekiya mfumu ya Yuda ndipo ukamuwuze kuti Yehova akuti mzinda uno ndidzawupereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni ndipo adzawutentha ndi moto. Iweyo sudzapulumuka mʼmanja mwake koma udzagwidwa ndithu ndipo adzakupereka mʼmanja mwake. Udzayiona mfumu ya ku Babuloni maso ndi maso ako ndipo udzayankhula nayo pakamwa ndi pakamwa. Ndipo udzapita ku Babuloni.
“Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva lonjezo ili la Yehova. Izi ndi zimene Yehova akunena za iwe: Sudzaphedwa pa nkhondo; udzafera pa mtendere. Monga anthu ankafukiza lubani poyika maliro a makolo ako akale, amene anali mafumu iwe usanalowe ufumu, choncho nawenso podzayika maliro ako adzafukiza lubani ndipo polira azidzati, ‘Kalanga, mbuye wanga!’ Ine mwini ndalonjeza zimenezi, akutero Yehova.”
Ndipo mneneri Yeremiya anawuza zonsezi Zedekiya mfumu ya Yuda, mu Yerusalemu. Nthawi imeneyi nʼkuti gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni likuthira nkhondo Yerusalemu ndi mizinda ina yotsala ya Yuda, Lakisi ndi Azeka. Imeneyi yokha ndiye inali mizinda yotetezedwa yotsala ya ku Yuda.
Kumasulidwa kwa Akapolo
Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya. Nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Zedekiya atachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze zakuti akapolo awo adzawamasule. Aliyense amene anali ndi akapolo a Chihebri, aamuna kapena aakazi awamasule; palibe amene ayenera kusunga mu ukapolo Myuda mnzake. Choncho akuluakulu pamodzi ndi anthu onse amene anachita pangano ili anagwirizana kuti amasule akapolo awo aamuna ndi aakazi ndi kuti asawasungenso mu ukapolo. Iwo anachitadi zimenezi ndipo anawamasuladi. Koma pambuyo pake anasintha maganizo awo ndi kuwatenganso amuna ndi akazi amene anawamasula aja ndipo anawasandutsanso akapolo.
Tsono Yehova anawuza Yeremiya kuti: “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Ine ndinachita pangano ndi makolo anu pamene ndinawatulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. Ine ndinati, ‘Chaka chachisanu ndi chiwiri chilichonse aliyense wa inu ayenera kumasula mʼbale wake wa Chihebri amene anadzigulitsa yekha kwa inuyo. Iyeyo amasulidwe akagwira ntchito zaka zisanu ndi chimodzi, mumulole apite mwaufulu.’ Komatu makolo anu sanandimvere kapena kusamala konse. Posachedwa pomwepa inu munalapa ndi kuchita zinthu zabwino pamaso panga: Aliyense wa inu anamasula mʼbale wake. Ndipo munachita pangano pamaso panga mʼNyumba imene imadziwika ndi dzina langa kuti mudzachitadi zimenezi. Koma tsopano mwasintha maganizo anu ndipo mwayipitsa dzina langa. Mwatenganso ukapolo aamuna ndi aakazi amene munawamasula aja kuti apite kumene akufuna. Mwawakakamiza kuti akhalebe akapolo anu.
“Nʼchifukwa chake Yehova akuti: Inu simunandimvere Ine; simunalengeze kuti abale anu amasulidwe. Chabwino! Ine ndidzakupatsani ufulu; ufulu wake ukhala wophedwa ndi nkhondo, mliri ndi njala. Ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha pakati pa maufumu onse a dziko lapansi. Inu simunasunge pangano limene munachita ndi Ine. Simunasamale lonjezo limene munachita pamaso panga. Choncho ndidzakusandutsani ngati mwana wangʼombe uja amene ankamudula pawiri napita pakati pa zigawozo. Amene ankadutsa pakati pa zigawozo anali atsogoleri a Yuda ndi Yerusalemu, akuluakulu a bwalo, ansembe ndi anthu onse a mʼdzikomo. Onsewa ndidzawapereka kwa adani awo amene akufuna kuwapha. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamlengalenga ndi zirombo za dziko lapansi.
“Ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda ndi nduna zake kwa adani awo amene akufuna kuwapha, kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni limene nthawi ino layamba kubwerera mʼmbuyo. Taonani, Ine ndidzawalamula, akutero Yehova, ndipo ndidzawabweretsanso ku mzinda uno. Adzathira nkhondo mzindawu, kuwulanda ndi kuwutentha. Ndipo Ine ndidzasandutsa chipululu mizinda ya Yuda kotero kuti palibe amene adzakhalemo.”
Arekabu
Yehova anayankhula ndi Yeremiya nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, kuti: “Pita ku banja la Arekabu ndipo ukawayitane kuti abwere mʼchipinda chimodzi cha Nyumba ya Yehova ndipo akafika uwapatse vinyo kuti amwe.”
Choncho ndinakatenga Yaazaniya (mwana wa Yeremiya winanso amene anali mwana wa Habaziniya), abale ake, ana ake onse aamuna ndi banja lonse la Arekabu. Ndinabwera nawo ku Nyumba ya Yehova, ku chipinda cha ophunzira a mneneri Hanani mwana wa Igidaliya, munthu wa Mulungu. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda cha akuluakulu, chimene chinali pamwamba pa chipinda cha Maaseya mwana wa Salumu, mlonda wa pa khomo. Kenaka ndinayika mabotolo odzaza ndi vinyo ndi zikho zake pamaso pa Arekabu ndipo ndinawawuza kuti, “Imwani vinyoyu.”
Koma iwo anayankha kuti, “Ife sitimwa vinyo, chifukwa kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula kuti, ‘Inuyo ngakhale zidzukulu zanu, musadzamwe vinyo mpaka kalekale. Musadzamange nyumba kapena kufesa mbewu, kapena kulima minda ya mpesa; musadzakhale ndi zinthu zimenezi. Mʼmalo mwake muzidzakhale mʼmatenti. Mukadzatero mudzakhala nthawi yayitali mʼdziko limene mukukhalamo.’ Ife takhala tikumvera zonse zimene kholo lathu Yehonadabu mwana wa Rekabu anatilamula. Ife ngakhale akazi athu kapena ana athu aamuna ndi aakazi sitinamwepo vinyo kapena kumanga nyumba kuti tizikhalamo kapenanso kukhala ndi minda ya mpesa, minda ina iliyonse kapena mbewu. Koma takhala mʼmatenti ndipo tamvera kwathunthu chilichonse chimene kholo lathu Yehonadabu anatilamula. Koma pamene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anathira nkhondo dziko lino, ife tinati, ‘Tiyeni tichoke, tipite ku Yerusalemu kuti tithawe magulu ankhondo a Akasidi ndi Aaramu.’ Kotero ife takhala tikukhala mu Yerusalemu.”
Yehova anayankhulanso ndi Yeremiya kuti, “Iyeyu, Yehova Mulungu wa Israeli anawuza Yeremiya kuti: Pita ukawawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Kodi simungatengeko phunziro ndi kumvera mawu anga?’ akutero Yehova. ‘Yehonadabu mwana wa Rekabu analamula ana ake kuti asamwe vinyo ndipo lamulo limeneli alisunga. Mpaka lero lino iwo samwa vinyo, chifukwa akumvera lamulo la kholo lawo. Koma Ine ndakhala ndikuyankhula nanu kawirikawiri kukuchenjezani, koma inu simunandimvere Ine. Kawirikawiri ndakhala ndikutumiza atumiki anga, aneneri, kwa inu. Iwo akhala akukuwuzani kuti, ‘Aliyense wa inu asiye ntchito zake zoyipa ndi kukonza makhalidwe ake; musatsatire milungu ina ndi kumayitumikira. Pamenepo mudzakhala mʼdziko limene ndinakupatsani ndi makolo anu.’ Komabe inu simunasamale zimenezi kapena kundimvera Ine. Zidzukulu za Yehonadabu mwana wa Rekabu zakhala zikumvera lamulo limene kholo lawo anazilamula, koma inuyo simunandimvere Ine.
“Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndidzagwetsera pa Yuda ndi pa onse okhala mu Yerusalemu masautso onse amene ndinakonza chifukwa sanandimvere. Ndinawayitana koma iwo sanayankhe.’ ”
Yeremiya anawuza banja la Arekabu mawu onse a Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, kuti, “Munamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mwatsatira malangizo ake onse ndi kuchita chilichonse chimene anakulamulani.” Tsono Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Yehonadabu mwana wa Rekabu sadzasowa munthu wonditumikira Ine nthawi zonse.”
Yehoyakimu Atentha Buku la Yeremiya
Chaka chachinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Tenga buku ndipo ulembemo mawu onse amene ndayankhula nawe otsutsa Israeli, Yuda ndi mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthawi imene ndinayamba kuyankhula nawe pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya mpaka lero lino. Mwina mwake anthu a ku Yuda adzamva za zoopsa zonse zimene ndakonza kuti ndiwachitire, ndipo munthu aliyense adzatembenuka ndi kusiya ntchito zake zoyipa. Motero ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndi machimo awo.”
Tsono Yeremiya anayitana Baruki mwana wa Neriya. Baruki analemba mʼbuku mawu onse amene Yeremiya ankamuwuza, mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya. Kenaka Yeremiya anawuza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Mulungu. Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo. Mwina mwake adzapempha kwa Yehova ndipo aliyense adzatembenuka ndi kusiya makhalidwe ake oyipa pakuti mkwiyo ndi ukali wa Yehova pa anthu awa ndi woopsa kwambiri.”
Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo. Pa mwezi wachisanu ndi chinayi wa chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, anthu onse a mu Yerusalemu ndi onse amene anabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, anapangana za kusala kudya kuti apepese Yehova. Atayima pa chipinda cha Gemariya mwana wa mlembi Safani, chimene chinali mʼbwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano cholowera ku Nyumba ya Yehova, Baruki anawerenga mawu onse a Yeremiya amene anali mʼbuku muja kwa anthu onse amene anali ku Nyumba ya Yehova.
Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova ochokera mʼbukumo, anapita ku nyumba ya mfumu nakalowa ku chipinda cha mlembi. Akuluakulu, mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akibori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya pamodzi ndi akuluakulu ena onse, anali atasonkhana kumeneko. Tsono Mikaya anawafotokozera mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga buku lija anthu onse akumva. Pambuyo pake akuluakulu onsewo anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuwuza kuti, “Bwera ndi buku limene unawerenga kwa anthu.” Ndipo Baruki mwana wa Neriya anapita nalo bukulo kwa anthuwo. Iwo anati, “Khala pansi, ndipo tiwerengere bukuli.”
Ndipo Baruki anawawerengera. Atamva mawu onsewo, anayangʼanana mwa mantha ndipo anamuwuza Baruki kuti, “Ndithudi tikafotokozera mfumu mawu onsewa.” Tsono anamufunsa Baruki kuti, “Tatiwuze, unalemba bwanji mawu onsewa? Kodi ndi Yeremiya anakulembetsa zimenezi?”
Baruki anayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiya amene anandiwuza mawu onsewa, ndipo ine ndinawalemba ndi utoto mʼbukumu.”
Kenaka akuluakuluwo anamuwuza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiya, pitani mukabisale. Munthu aliyense asadziwe kumene muli.”
Atayika bukulo mʼchipinda cha mlembi Elisama, analowa mʼbwalo, napita kwa mfumu ndi kukayifotokozera zonse. Itamva zimenezi mfumu inatuma Yehudi kuti akatenge bukulo, ndipo Yehudi anakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama ndipo anawerengera mfumu pamodzi ndi akuluakulu ake amene anali naye. Unali mwezi wachisanu ndi chinayi ndipo mfumu inali mʼnyumba ya pa nyengo yozizira, ikuwotha moto umene anasonkha. Yehudi ankati akawerenga masamba atatu kapena anayi a bukulo, mfumu inkawangʼamba ndi mpeni ndi kuwaponya pa moto ndipo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka buku lonse linapsa. Mfumu pamodzi ndi omutumikira ake onse amene anamva mawu onsewa sanachite mantha kapena kungʼamba zovala zawo. Ngakhale kuti Elinatani, Delaya, ndi Gemariya anapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, mfumuyo sinawamvere. Mʼmalo mwake, mfumu inalamula Yerahimeeli mwana wake, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti agwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma pamenepo nʼkuti Yehova atawabisa.
Mfumu itatentha buku limene linali ndi mawu amene Yeremiya anamulembetsa Baruki, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Tenganso buku lina ndipo ulembe mawu onse amene anali mʼbuku loyamba lija, limene Yehoyakimu analitentha. Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’ Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku. Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.”
Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.
Atsekera Yeremiya Mʼndende
Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, inakhazika pa mpando waufumu Zedekiya mwana wa Yosiya kukhala mfumu ya Yuda. Iye analowa mʼmalo mwa Yehoyakini mwana wa Yehoyakimu. Koma Zedekiya kapena atumiki ake ngakhalenso anthu a mʼdzikomo sanasamalire mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa mneneri Yeremiya.
Tsono Zedekiya anatuma Yehukali mwana wa Selemiya ndi wansembe Zefaniya mwana wa Maseya kwa mneneri Yeremiya ndi uthenga uwu: “Chonde tipempherereni kwa Yehova Mulungu wathu.”
Nthawi imeneyinso nʼkuti Yeremiya ali ndi ufulu woyenda pakati pa anthu chifukwa anali asanaponyedwe mʼndende. Nthawi imeneyinso nʼkuti gulu lankhondo la Farao litatuluka mʼdziko la Igupto. Ndipo Ababuloni amene anali atazinga Yerusalemu atamva zimenezi, anachoka ku Yerusalemuko.
Tsono Yehova anawuza mneneri Yeremiya kuti, “Uyiwuze mfumu ya Yuda imene inakutuma kuti udzapemphe nzeru kwa ine kuti Ine Yehova, Mulungu wa Israeli ndikuti, gulu lankhondo la Farao limene linatuluka kuti lidzakuthandize lidzabwerera kwawo ku Igupto. Ndipo Ababuloni adzabwerera kudzathira nkhondo mzinda uno. Iwo adzawugonjetsa ndi kuwutentha.
“Yehova akuti: Musadzinyenge, nʼkumaganiza kuti, ‘Ndithu Ababuloni adzatisiya.’ Ndithudi sadzakusiyani! Ngakhale mutagonjetsa gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene likukuthirani nkhondo ndipo mʼmatenti mwawo ndikutsala anthu ovulala okhaokha, amenewo adzabwera ndi kudzatentha mzinda uno.”
Gulu lankhondo la Ababuloni litaleka kuthira nkhondo mzinda wa Yerusalemu chifukwa choopa gulu lankhondo la Farao, Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu ndi kumapita ku dziko la Benjamini kuti akalandire gawo lake la minda ya makolo ake. Koma atafika pa Chipata cha Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anagwira mneneri Yeremiyayo ndipo anati, “Iwe ukuthawira kwa Ababuloni!”
Yeremiya anati, “Zimenezo si zoona! Ine sindikuthawira kwa Ababuloni.” Koma Iriya sanamumvere. Mʼmalo mwake anagwira Yeremiya nʼkupita naye kwa akuluakulu. Akuluakuluwo anamupsera mtima Yeremiya ndipo anamukwapula ndi kumuyika mʼnyumba ya mlembi Yonatani, imene anayisandutsa ndende.
Yeremiya anayikidwa mʼndende ya pansi pa nthaka, kumene anakhalako nthawi yayitali. Kenaka Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akayitane Yeremiya ndipo anabwera naye ku nyumba ya mfumu. Atafika mfumu inamufunsa mwamseri kuti, “Kodi pali mawu ena amene Yehova wakuwuza?”
Yeremiya anayankha kuti, “Inde. Inu mfumu mudzaperekedwa kwa mfumu ya ku Babuloni.”
Pamenepo Yeremiya anafunsa Mfumu Zedekiya kuti, “Kodi ndakulakwirani chiyani inuyo kapena akuluakulu anu kapenanso anthu awa, kuti mundiyike mʼndende? Kodi ali kuti aneneri anu amene anakuloserani kuti, ‘Mfumu ya ku Babuloni sidzakuthirani nkhondo pamodzi ndi dziko lino’? Koma tsopano, mbuye wanga mfumu, chonde tamverani. Loleni ndinene pempho langa pamaso panu: Musandibwezere ku nyumba ya mlembi Yonatani, kuopa kuti ndingakafere kumeneko.”
Tsono Mfumu Zedekiya analamula kuti Yeremiya asungidwe mʼbwalo la alonda. Ankamupatsa buledi tsiku ndi tsiku amene ankamugula kwa ophika buledi. Anapitiriza kutero mpaka buledi yense anatha mu mzindamo. Choncho Yeremiya anapitirira kukhala mʼbwalo la alonda.
Yeremiya Aponyedwa Mʼchitsime cha Matope
Sefatiya mwana wa Matani, Gedaliya mwana wa Pasi-Huri, Yukali mwana wa Selemiya, ndi Pasi-Huri mwana wa Malikiya anamva zimene Yeremiya ankawuza anthu onse kuti, “Yehova akuti, ‘Aliyense amene akhale mu mzinda muno adzafa ndi nkhondo njala kapena mliri. Koma aliyense amene atatuluke kukadzipereka kwa Ababuloni adzapulumutsa moyo wake; iyeyo adzakhala ndi moyo. Mzinda uno udzaperekedwa ndithu kwa gulu lankhondo la mfumu ya ku Babuloni, amene adzawulande.’ ”
Tsono akuluakuluwo anawuza mfumu kuti, “Munthu uyu ayenera kuphedwa. Iye akutayitsa mtima asilikali pamodzi ndi anthu onse amene atsala mu mzinda muno, chifukwa cha zimene akuwawuza. Munthu ameneyu sakufunira zabwino anthuwa koma chiwonongeko chawo.”
Mfumu Zedekiya anayankha kuti, “Munthuyu ali mʼmanja mwanu. Ine sindingakuletseni chimene mukufuna kumuchitira.”
Choncho iwo anatenga Yeremiya nakamuponya mʼchitsime cha Malikiya, mwana wa mfumu, chimene chinali mʼbwalo la alonda. Iwo anamutsitsira mʼdzenjemo ndi chingwe. Munalibe madzi koma matope okhaokha, ndipo Yeremiya anamira mʼmatopewo.
Koma Ebedi-Meleki, Mkusi, mmodzi mwa anthu ofulidwa ogwira ntchito mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya anamuponya mʼchitsime. Nthawi imeneyo nʼkuti mfumu ili ku chipata cha Benjamini. Ebedi-Meleki anatuluka ku nyumba ya mfumu kukayiwuza kuti, “Mbuye wanga mfumu, zimene anthu awa amuchitira mneneri Yeremiya ndi zoyipa kwambiri. Iwo amuponya mʼchitsime, ndipo adzafa ndi njala chifukwa buledi watha mu mzinda muno.”
Tsono mfumu inalamula Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, “Tenga anthu makumi atatu, ndipo mukamutulutse mʼchitsimemo mneneri Yeremiya asanafe.”
Pamenepo Ebedi-Meleki anatenga anthuwo, napita nawo ku nyumba ya mfumu ya pansi pa chipinda chosungiramo chuma. Kumeneko anakatengako sanza ndipo anatsitsira sanzazo ndi chingwe mʼchitsime mʼmene munali Yeremiya. Ebedi-Meleki, Mkusi, anawuza Yeremiya kuti, “Ika sanzazo mkwapa mwako kuti zingwe zingakupweteke.” Yeremiya anachitadi zimenezi, ndipo anamukoka ndi zingwe ndi kumutulutsa mʼchitsimecho. Ndipo Yeremiya anakhalabe ku bwalo la alonda.
Zedekiya Afunsanso Yeremiya
Tsiku lina Mfumu Zedekiya anayitana mneneri Yeremiya ndipo anabwera naye ku chipata chachitatu cha Nyumba ya Yehova. Mfumu inawuza Yeremiya kuti, “Ndikufuna kukufunsa kanthu kena, ndipo usandibisire chilichonse.”
Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Ndikakuyankhani, kodi simundipha? Ngakhaletu ine nditakulangizani, inu simudzandimvera.”
Koma Mfumu Zedekiya mwachinsinsi inalumbira kwa Yeremiya kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene amatipatsa moyo, sindidzakupha ngakhalenso kukupereka kwa amene akufuna kukuphawa.”
Pamenepo Yeremiya anati kwa Zedekiya, “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ngati mutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mudzakhala ndi moyo ndipo mzinda uno sadzawutentha, inu pamodzi ndi banja lanu mudzakhala ndi moyo. Koma ngati simutuluka kukadzipereka kwa ankhondo a mfumu ya ku Babuloni, mzinda uno udzaperekedwa kwa Ababuloni ndipo adzawutentha; inuyo simudzapulumuka mʼdzanja mwawo.’ ”
Mfumu Zedekiya inati kwa Yeremiya, “Ine ndikuopa Ayuda amene anathawira kale kwa Ababuloni, pakuti mwina Ababuloniwo adzandipereka kwa Ayudawo ndipo iwowo adzandizunza.”
Yeremiya anayankha kuti, “Ngati mumvera Yehova ndi kuchita zimene ndakuwuzani, ndiye kuti zinthu zidzakuyenderani bwino. Inu simudzaphedwa. Koma mukakana kudzipereka, chimene Yehova wandiwululira ndi ichi: Akazi onse amene atsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda adzaperekedwa kwa akuluakulu a mfumu ya ku Babuloni. Akazi amenewo adzakuwuzani kuti,
“ ‘Abwenzi ako okhulupirika aja anakusokeretsa,
ndipo anakugonjetsa.
Poti tsopano miyendo yako yazama mʼmatope;
abwenzi ako aja akusiya.’
“Akazi pamodzi ndi ana anu adzaperekedwa kwa Ababuloni. Inuyo simudzapulumuka mʼmanja mwawo koma mfumu ya ku Babuloni idzakugwirani; mzinda uno adzawutentha.”
Pamenepo Zedekiya anati kwa Yeremiya, “Usawuze munthu wina aliyense zimene takambiranazi, ukatero udzaphedwa. Akuluakulu akamva kuti ndinayankhula nawe ndipo akabwera kwa iwe nʼkudzakufunsa kuti, ‘Tiwuze zimene unanena kwa mfumu ndi zimene mfumu inanena kwa iwe; usatibisire, ukatero tidzakupha,’ udzawawuze kuti, ‘Ine ndimapempha mfumu kuti isandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani kuti ndikafere kumeneko.’ ”
Akuluakulu onse anabweradi kwa Yeremiya kudzamufunsa. Iye anawayankha monga momwe mfumu inamulamula. Choncho palibe amene ananenanso kanthu, pakuti palibe amene anamva zomwe anakambirana ndi mfumu.
Ndipo Yeremiya anakhalabe mʼbwalo la alonda mpaka tsiku limene mzinda wa Yerusalemu unalandidwa.
Kugonjetsedwa kwa Yerusalemu
Mzinda wa Yerusalemu anawulanda motere: Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawuzinga mzindawo. Ndipo pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, malinga a mzindawo anabowoledwa. Pamenepo akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anabwera nakakhala pa Chipata Chapakati. Akuluwo ndi awa: Nerigali-Sarezeri, Samugara Nebo, Sarisekimu mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri winanso mlangizi wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni. Zedekiya mfumu ya Yuda pamodzi ndi ankhondo ake atawaona, anathawa mu mzindawo usiku podzera ku munda wa mfumu, kudutsa chipata cha pakati pa makoma awiri. Anathawira ku Araba.
Koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola ndi kumupeza Zedekiyayo mʼchigwa cha ku Yeriko. Anamugwira napita naye kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati kumene anagamula mlandu wake. Ku Ribulako, mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona. Inaphanso anthu olemekezeka onse a ku Yuda. Kenaka inakolowola maso a Zedekiya ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni.
Ababuloni anatentha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu, ndiponso anagwetsa malinga a Yerusalemu. Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu, anatenga ukapolo anthu onse otsala mu mzindamo kupita nawo ku Babuloni, pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa iye. Koma Nebuzaradani, mtsogoleri wa alonda ankhondo anasiya mʼdziko la Yuda anthu ena osauka, amene analibe chilichonse; ndipo anawapatsa minda ya mpesa ndi minda inanso.
Tsono Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni inatuma mawu kwa Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda ankhondo a mfumu za Yeremiya. Iye anati: “Mutenge, umusamale bwino, ndipo usamuvute koma umuchitire zimene afuna.” Choncho Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda, Nebusazibani mkulu wa nduna, Nerigali-Sarezeri mlangizi wamkulu wa mfumu ndi akuluakulu onse a mfumu ya ku Babuloni anatuma anthu nakamutulutsa Yeremiya mʼbwalo la alonda. Anakamupereka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kuti amutumize ku nyumba yake. Ndipo Yeremiya anakhala pakati pa abale ake.
Yeremiya ali mʼndende ku bwalo la alonda, Yehova anayankhula naye: “Pita ukamuwuze Ebedi-Meleki, Mkusi, kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Zidzachitikadi zimene ndinanena zokhudza mzinda uno; ndipo zidzakhala zoyipa osati zabwino ayi. Zimenezi zidzachitika pa nthawi yake iwe ukuona. Koma ndidzakupulumutsa pa tsiku limenelo, akutero Yehova; sudzaperekedwa kwa anthu amene umawaopa. Ndithu ndidzakupulumutsa; sudzaphedwa pa nkhondo koma udzapulumuka, chifukwa wadalira Ine, akutero Yehova.’ ”
Amasula Yeremiya
Yehova anayankhula ndi Yeremiya pamene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anamasula Yeremiyayo ku Rama. Anamupeza Yeremiya ali womangidwa ndi unyolo pamodzi ndi amʼndende ena onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene ankapita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Mtsogoleriyu anamupeza Yeremiya, anamuwuza kuti, “Yehova Mulungu wako analengeza kale zakuti malo ano adzawonongedwa. Ndipo tsopano Yehova wachitadi zimenezi monga mmene ananenera. Izi zonse zachitika chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamumvere. Koma tsopano taona, lero ndikukumasula unyolo umene unali mʼmanja mwako. Ngati ukufuna kupita nane ku Babuloni, tiye ndipo adzakusamala bwino. Koma ngati sukufuna kupita, ndiye usapite. Dziko ndi limeneli monga ukulioneramo. Uli ndi ufulu kupita kulikonse kumene ukufuna.” Yeremiya asanayankhe, Nebuzaradani anamuwuzanso kuti, “Ngati supita ndiye pita, ubwerere kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kuti akhale bwanamkubwa wa Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthu, kapena upite kulikonse ukufuna.”
Ndipo mtsogoleri uja anamupatsa Yeremiya chakudya ndi mphatso zina ndi kumulola kuti apite. Motero Yeremiya anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa ndipo anakakhala naye kumeneko pakati pa anthu amene anatsala mʼdzikomo.
Kuphedwa kwa Gedaliya
Panali atsogoleri ena a nkhondo ndi anthu awo amene sanadzipereke nawo. Iwowa anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu kukhala bwanamkubwa wa dzikolo ndipo kuti yamuyika kukhala wolamulira amuna, akazi ndi ana amene anali osauka kwambiri mʼdzikomo, amene sanawagwire ukapolo kupita nawo ku Babuloni. Iwowa anapita ku Mizipa kwa Gedaliya. Amene anapitawo ndi awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti, ana a Efai a ku Netofa, ndi Yezaniya mwana wa Maaka, iwowo pamodzi ndi anthu awo. Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani, anawalonjeza iwo pamodzi ndi anthuwo mwalumbiro. Ndipo anati, “Musaope kuwatumikira Ababuloni. Khalani mʼdziko muno, tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino. Ine ndidzakhala ku Mizipa kuti ndizikuyimirirani kwa Ababuloni amene azidzabwera kwa ife, koma inu muzikolola vinyo wanu, zipatso zanu, mafuta anu ndi kuzisunga mʼmitsuko yanu, nʼkumakhala mʼmizinda imene mwalandayo.”
Nawonso Ayuda onse a ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu ndi a ku mayiko ena onse anamva kuti mfumu ya ku Babuloni inasiyako anthu ena ku Yuda ndipo kuti inasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala bwanamkubwa wawo. Tsono Ayuda onsewo anabwerera ku Yuda, ku Mizipa kwa Gedaliya, kuchokera ku mayiko onse kumene anabalalikira. Ndipo anakolola zipatso zochuluka ndi vinyo wambiri.
Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri a ankhondo onse amene sanadzipereke aja anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya Aamoni watuma Ismaeli mwana wa Netaniya kuti akuphe?” Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawankhulupirire.
Tsono Yohanani mwana wa Kareya, mwamseri anawuza Gedaliya ku Mizipa kuti, “Loleni ndipite ndikaphe Ismaeli mwana wa Netaniya, ndipo palibe amene ati adziwe. Akuphereninji ndi kuchititsa Ayuda onse, amene akuzungulirani kuti abalalike ndi kuti otsala a ku Yuda awonongeke?”
Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu anawuza Yohanani mwana wa Kareya kuti, “Usachite zimenezo! Zimene ukunena za Ismaeli ndi zabodza.”
Pa mwezi wachisanu ndi chiwiri Ismaeli mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama amene anali wa banja laufumu ndiponso mmodzi wa atsogoleri a ankhondo a mfumu, anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ndi anthu khumi. Pamene ankadya naye kumeneko, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu khumi aja anayimirira ndi kupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Choncho anapha munthu amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kukhala bwanamkubwa wa dzikolo. Ismaeli anaphanso Ayuda onse amene anali pamodzi ndi Gedaliya ku Mizipa, kuphatikizanso asilikali a Ababuloni amene anali ku Mizipako.
Mmawa mwake, anthu asanadziwe kuti Gedaliya waphedwa, kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova. Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.” Atafika pakati pa mzinda, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu amene anali naye anawapha anthuwo ndi kuwaponya mʼchitsime. Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja. Tsono chitsime chimene anaponyamo mitembo ya anthu amene anawaphawo pamodzi ndi mtembo wa Gedaliya chinali chimene mfumu Asa anachikumba poopsedwa ndi Baasa mfumu ya Israeli. Ismaeli mwana wa Netaliya anachidzaza ndi mitembo.
Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni.
Pamene Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye pamodzi anamva zoyipa zonse zimene Ismaeli mwana wa Netaniya anachita, anatenga ankhondo awo onse kupita kukamenyana ndi Ismaeli mwana wa Netaniya. Anakamupeza kufupi ndi chidziwe chachikulu cha ku Gibiyoni. Pamene anthu onse amene Ismaeli anawagwira anaona Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali naye, anasangalala. Anthu onse amene Ismaeli anawagwira ukapolo ku Mizipa anabwerera ndi kupita kwa Yohanani mwana wa Kareya. Koma Ismaeli pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, anathawa Yohanani ndi kuthawira kwa Aamoni.
Kuthawira ku Igupto
Kenaka Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye anatsogolera anthu onse otsala a ku Mizipa amene anawapulumutsa kwa Ismaeli mwana wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Anthu amenewa anali: asilikali, akazi, ana ndi amuna ofulidwa otumikira mfumu amene anawatenga ku Gibiyoni. Ndipo ananyamuka nayima ku Geruti Kimuhamu pafupi ndi Betelehemu pa ulendo wawo wopita ku Igupto kuthawa Ababuloni. Iwo anaopa Ababuloniwo chifukwa Ismaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babuloni inamuyika kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.
Atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya ndi Azariya mwana wa Hosayia, ndiponso anthu onse, ana ndi akuluakulu omwe, anapita kwa mneneri Yeremiya ndipo anamuwuza kuti, “Chonde imvani dandawulo lathu ndipo mutipempherere anthu otsalafe kwa Yehova Mulungu wanu. Pakuti monga tsopano mukuona, ngakhale kuti kale tinalipo ambiri, koma tsopano ochepa okha ndiye amene atsala. Mupemphere kuti Yehova Mulungu wanu atiwuze kumene tiyenera kupita ndi chimene tiyenera kuchita.”
Mneneri Yeremiya anawayankha kuti, “Ndamva zimene mwanenazi. Ndithu ndidzapemphera kwa Yehova Mulungu wanu monga momwe mwandipemphera. Ndidzakuwuzani chilichonse chimene Yehova anene ndipo sindidzakubisirani kanthu kalikonse.”
Ndipo iwo anawuza Yeremiya kuti, “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika yodzatitsutsa ife ngati sitichita mogwirizana ndi chilichonse chimene Yehova Mulungu adzakutumani kuti mutiwuze. Kaya ndi zotikomera kapena zosatikomera, ife tidzamvera Yehova Mulungu wathu, amene takutumaniko. Tidzamvera Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zidzatiyendere bwino.”
Patapita masiku khumi, Yehova anayankhula ndi Yeremiya. Choncho Yeremiya anayitana Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye ndiponso anthu onse, ana ndi akulu omwe. Yehova, Mulungu wa Israeli amene munanditumako kuti ndikapereke madandawulo mʼdzina lanu akuti, “Ngati mukhala mʼdziko muno, ndiye kuti ndidzakukhazikitsani, osakuchotsani. Inde ndidzakudzalani osakuchotsani pakuti ndi kumva chisoni kwambiri chifukwa cha mavuto amene ndabweretsa pa inu. Musayiope mfumu ya ku Babuloni, imene mukuyiopa tsopano. Musachite nayo mantha, akutero Yehova, pakuti Ine ndili nanu ndipo ndidzakupulumutsani ndi kukulanditsani mʼmanja mwake. Ndidzakuchitirani chifundo, ndipo mfumuyonso idzakuchitirani chifundo ndi kukulolani kuti mukhale mʼdziko mwanumwanu.
“Koma mwina simudzamvera Yehova Mulungu wanu nʼkumanena kuti, ‘Ayi ife sitidzakhala mʼdziko muno, ndipo ngati mukunena kuti, ‘Ayi, koma tidzapita ku Igupto kumene sitidzaonako nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga kapenanso kusowa chakudya.’ Tsono, inu otsala a ku Yuda, imvani mawu a Yehova. Iye akuti, ngati mutsimikiza zopita ku Igupto, nʼkupitadi kukakhala kumeneko, ndiye nkhondo imene mukuyiopayo idzakugonjetsani ku Igupto komweko. Njala imene mukuyiopayo idzakupezani ku Igupto komweko ndipo mudzafera kumeneko. Kunena zoona, onse amene atsimikiza zopita ku Igupto kuti akakhale kumeneko adzafa ndi nkhondo njala ndi mliri. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzapulumuke kapena kuthawa mavuto amene ndidzawagwetsera.’ Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Momwe ndinawakwiyira mwaukali anthu okhala mu Yerusalemu, koteronso ndidzakukwiyirani mukapita ku Igupto. Mudzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, choseketsa ndi chonyozeka. Malo ano simudzawaonanso.’
“Inu otsala a ku Yuda, Yehova wakuwuzani kuti, ‘Musapite ku Igupto.’ Dziwani chinthu ichi: Ine lero ndikukuchenjezani kuti munalakwitsa kwambiri. Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu nʼkumati ‘Mukatipempherere kwa Yehova Mulungu wathu, nʼkudzatiwuza chimene afuna kuti tichite, ndipo ife tidzachita.’ Ine lero ndakuwuzani, koma inu simukumverabe zonse zimene Yehova Mulungu anandituma kuti ndikuwuzeni. Tsono dziwani ichi: mudzafadi ndi nkhondo, njala ndi mliri kumalo kumene mukufuna mukakhaleko.”
Yeremiya atatsiriza kuwawuza anthuwo mawu onse a Yehova Mulungu wawo, amene Yehova anamutuma kuti akawawuze, Azariya mwana wa Hosayia ndi Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi anthu onse odzikuza anawuza Yeremiya kuti, “Ukunama iwe! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti unene kuti, ‘Musapite ku Igupto kukakhala kumeneko.’ Koma ndi Baruki mwana wa Neriya amene akukulimbikitsa kuti utiletse zopita ku Igupto ndi kuti mʼmalo mwake tidzipereke mʼmanja mwa Ababuloni, kuti iwo atiphe kapena kutitenga ukapolo ku Babuloni.”
Motero Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo pamodzi ndi anthu onse sanamvere lamulo la Yehova loti akhale mʼdziko la Yuda. Mʼmalo mwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo anatenga anthu onse otsala a ku Yuda amene anabwera kudzakhala mʼdziko la Yuda kuchokera ku mayiko onse kumene anabalakirako. Mʼgulu la anthu otengedwalo munali amuna onse, akazi ndi ana, ana aakazi a mfumu, ndiponso anthu amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anawasiya kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani pamodzinso ndi mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya. Kotero anthuwo analowa mʼdziko la Igupto chifukwa anakana kumvera Yehova, nakafika ku Tapanesi.
Ndipo Yehova anayankhula ndi Yeremiya ku Tapanesi kuti, “Tenga miyala inayi yayikulu ndipo uyikwirire mʼdothi pa chiwundo cha polowera ku nyumba yaufumu ya Farao ku Tapanesi. Uchite zimenezi Ayuda onse akuona. Ndipo uwawuze kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Ndidzayitana mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, ndipo adzakhazika mpando wake waufumu pa miyala imene ndayikwirira apayi. Iye adzafunyulula tenti yake yaufumu pa miyala imeneyi. Iye adzabwera kudzathira nkhondo Igupto. Iwo oyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri, iwo oyenera kutengedwa ukapolo adzatengedwa ukapolo, ndipo iwo oyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga. Adzayatsa moto mʼnyumba zopembedzera milungu ya Igupto. Adzayeretsa dziko la Igupto monga momwe mʼbusa amayeretsera chovala chake pochotsamo nsabwe. Pambuyo pake adzachoka mʼdziko la Igupto mwa mtendere. Ku Iguptoko adzagwetsa zipilala zachipembedzo za ku nyumba yopembedzera mulungu wa dzuwa. Adzatentha ndi moto nyumba za milungu ya ku Igupto.’ ”
Masautso Chifukwa cha Kupembedza Mafano
Uthenga umene Yeremiya analandira wonena za Ayuda onse amene ankakhala ku Igupto, ku mizinda ya Migidoli, Tapanesi ndi Mefisi, ndiponso ku Patirosi ndi uwu: “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu mwaona mavuto aakulu amene ndinawabweretsa pa Yerusalemu ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda yonseyo yasanduka mabwinja, yopanda munthu wokhalamo. Zimenezi zinachitika chifukwa cha zoyipa zomwe anachita. Iwo anaputa mkwiyo wanga pofukiza lubani ndi potumikira milungu ina imene iwo kapena inu ngakhalenso makolo anu sanayidziwe. Kawirikawiri Ine ndakhala ndikutuma atumiki anga, aneneri, amene anati, ‘Musachite chinthu chonyansachi chimene Ine ndimadana nacho!’ Koma iwo sanamvere kapena kulabadira; sanatembenuke kusiya zoyipa zawo kapena kuleka kufukiza lubani kwa milungu ina. Nʼchifukwa chake mkwiyo wanga unayaka ngati moto kutentha mizinda ya ku Yuda ndi misewu ya mu Yerusalemu ndi kuyisandutsa bwinja mpaka lero.
“Ndiye tsopano Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, ‘Chifukwa chiyani mukufuna kudziwononga chotere? Kodi mukufuna kuti amuna, akazi, ana ndi makanda onse aphedwe ndi kuti mu Yuda musatsale ndi munthu mmodzi yemwe? Chifukwa chiyani mukuputa mkwiyo wanga popembedza mafano pofukiza lubani kwa milungu ina mʼdziko lino la Igupto mʼmene mukukhalamo. Kodi mukuchita zimenezi kuti mudziwononge nokha ndi kuti mudzisandutse chinthu choseketsa ndi chonyozeka pakati pa mitundu yonse ya dziko lapansi? Kodi mwayiwala zoyipa zimene anachita makolo anu, mafumu a ku Yuda ndi akazi awo, ndiponso zoyipa zimene munachita inuyo ndi akazi anu mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? Koma mpaka lero simunalape. Simunandilemekeze kapena kumvera malamulo anga amene ndinayikira inuyo ndi makolo anu.
“Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akunena kuti, ‘Ine ndatsimikiza zobweretsa mavuto pa inu ndi kuwatheratu anthu a ku Yuda. Ndidzatenga anthu otsala a ku Yuda amene atsimikiza zopita ku Igupto ndi kukakhala kumeneko. Onse adzathera ku Igupto. Adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, adzaphedwa ndi lupanga kapena kufa ndi njala. Adzasanduka chinthu chotembereredwa ndi chochititsa mantha, chinthu choseketsa ndi chonyozeka. Ndidzalanga Ayuda okhala ku Igupto ndi lupanga, njala ndi mliri, ngati mmene ndinalangira anthu a ku Yerusalemu. Motero mwa anthu amene anapita ku Igupto palibe ndi mmodzi yemwe adzapulumuke, kapena kukhala ndi moyo, kapena kubwerera ku Yuda. Palibe amene adzabwerere kupatula othawa nkhondo.’ ”
Tsono amuna onse amene anadziwa kuti akazi awo ankafukiza lubani kwa milungu ina, ndiponso akazi onse amene anali pamenepo, gulu lalikulu la anthu, pamodzi ndi anthu onse amene amakhala ku Patirosi mʼdziko la Igupto, anati kwa Yeremiya, “Ife sitimvera uthenga umene watiwuza mʼdzina la Yehova! Koma tidzachitadi chilichonse chimene tinanena kuti tidzachita: Tidzafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndipo tidzayipatsa nsembe yachakumwa ngati mmene tinkachitira ifeyo ndi makolo athu, mafumu athu ndi akuluakulu mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu. Nthawi imeneyo ife tinali ndi chakudya chochuluka ndipo tinali pabwino, sitimapeza mavuto. Koma kuchokera nthawi imene tinasiya kufukiza lubani ndi kupereka chopereka cha chakumwa kwa mfumukazi yakumwamba, ifeyo takhala tikusowa zinthu ndipo takhala tikuphedwa ndi lupanga ndi kufa ndi njala.”
Akazi anawonjezera kunena kuti, “Pamene tinkafukiza lubani kwa mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa, kodi suja amuna athu ankavomereza mmene timayipangira mfumukazi yakumwambayo makeke abwino olembapo chinthunzi chake ndi kuyipatsa chopereka cha chakumwa?”
Yeremiya atamva kuyankha kumeneku anawawuza kuti, “Kodi mukuganiza kuti Yehova nʼkuyiwala kuti inuyo ndi makolo anu, mafumu anu ndi akuluakulu anu, ndiponso anthu onse, munkafukiza lubani kwa mafano a mʼmizinda ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? Ndiye Yehova sakanathanso kupirira ndi machitidwe anu ndi zonyansa zimene munkachita. Nʼchifukwa chake dziko lanu linasanduka chipululu, chinthu choopsa ndi chotembereredwa. Dziko lopandamo anthu monga zilili lero lino. Mavuto awa akugwerani chifukwa munkafukiza lubani ndipo munkachimwira Yehova pokana kumvera mawu ake ndi kutsatira malamulo ndi malangizo ake.”
Kenaka Yeremiya anawuza anthu onse, makamaka akazi kuti, “Imvani mawu a Yehova, anthu onse a ku Yuda amene muli mu Igupto. Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Inu ndi akazi anu munalonjeza ndi pakamwa panu, ndipo malonjezowo mwakwaniritsa. Inu munanena kuti, ‘Tidzachita zimene tinalonjeza, kufukizira lubani mfumukazi yakumwamba ndi kuyipatsa chopereka cha zakumwa.’ Tsopano chitanitu zimene munalonjezazo! Kwaniritsani malumbiro anu.
“Yambani, chitani zimene munalonjeza! Kwaniritsani malumbiro anu! Koma imvani mawu a Yehova, inu Ayuda nonse amene mukukhala mu Igupto: Yehova akuti, ‘Ine ndikulumbira mʼdzina langa lopambana kuti palibe wochokera ku Yuda amene akukhala mu Igupto amene adzatchule dzina langa polumbira kuti, ‘Pali Ambuye Yehova wamoyo.’ Pakuti ndionetsetsa kuti ndiwachitire choyipa, osati chabwino. Anthu a ku Yuda amene akukhala ku Igupto adzaphedwa pa nkhondo. Ena adzafa ndi njala mpaka onse atatheratu. Amene adzapulumuke ku lupanga ndi kubwerera ku dziko la Yuda kuchokera ku Igupto adzakhala ochepa kwambiri. Choncho otsala onse a ku Yuda amene anapita kukakhala ku Igupto adzadziwa kuti mawu woona ndi ati, anga kapena awo.
“Ine Yehova ndikukupatsani chizindikiro chakuti ndidzakulangani ku malo ano. Motero mudzadziwa kuti mawu anga akuti ndidzakulangani ndi woona. Yehova akuti, ‘Ine ndidzamupereka Farao Hofira mfumu ya Igupto kwa adani ake amene akufuna kumupha, monga momwe ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, mdani wake amene ankafuna kumupha.’ ”
Uthenga kwa Baruki
Uwu ndi uthenga umene mneneri Yeremiya anawuza Baruki mwana wa Neriya mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa mwana ya Yosiya kuti alembe mʼbuku. “Yehova Mulungu wa Israeli, akunena kwa iwe Baruki kuti: Iwe unati, ‘Kalanga ine! Yehova wawonjezera chisoni pa mavuto anga. Ine ndatopa ndi kubuwula ndipo sindikupeza mpumulo.’ ”
Koma Yehova akukuwuza kuti, “Ndidzagwetsa chimene ndinamanga ndipo ndidzazula chimene ndinadzala. Ndidzachita zimenezi mʼdziko lonse. Kodi tsono ukudzifunira wekha zinthu zazikulu? Usadzifunire. Pakuti ndidzagwetsa mavuto pa anthu onse, koma ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungadzapite.”
Yehova anamupatsa Yeremiya uthenga wonena za anthu a mitundu ina.
Uthenga Wonena za Igupto
Kunena za Igupto:
Yehova ananena za gulu lankhondo la Farao Neko mfumu ya ku Igupto limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni analigonjetsa ku Karikemesi ku mtsinje wa Yufurate mʼchaka cha chinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda,
anati, “Konzani zishango zanu ndi malihawo,
ndipo yambanipo kupita ku nkhondo!
Mangani akavalo,
ndipo kwerani inu okwerapo!
Khalani pa mzere
mutavala zipewa!
Nolani mikondo yanu,
valani malaya anu ankhondo!
Yeremiya anati: Kodi ndikuona chiyani?
Achita mantha
akubwerera,
ankhondo awo agonjetsedwa.
Akuthawa mofulumirapo
osayangʼananso mʼmbuyo,
ndipo agwidwa ndi mantha ponseponse,”
akutero Yehova.
Waliwiro sangathe kuthawa
ngakhale wankhondo wamphamvu sangathe kupulumuka.
Akunka napunthwa ndi kugwa
kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.
“Kodi ndani amene akukwera ngati Nailo,
ngati mtsinje wa madzi amkokomo?
Igupto akusefukira ngati Nailo,
ngati mitsinje ya madzi amkokomo.
Iye akunena kuti, ‘Ndidzadzuka ndi kuphimba dziko lapansi;
ndidzawononga mizinda ndi anthu ake.’
Tiyeni, inu akavalo!
Thamangani inu magaleta!
Tulukani, inu ankhondo,
ankhondo a ku Kusi ndi Puti amene mumanyamula zishango,
ankhondo a ku Ludi amene mumaponya uta.
Koma tsikulo ndi la Ambuye Yehova Wamphamvuzonse;
tsiku lolipsira, lolipsira adani ake.
Lupanga lake lidzawononga ndi kukhuta magazi,
lidzaledzera ndi magazi.
Pakuti Yehova, Yehova Wamphamvuzonse, adzapereka adani ake ngati nsembe
mʼdziko la kumpoto mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate.
“Pita ku Giliyadi ukatenge mankhwala
iwe namwali Igupto.
Wayesayesa mankhwala ambiri koma osachira;
palibe mankhwala okuchiritsa.
Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako;
kulira kwako kwadzaza dziko lapansi.
Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana,
onse awiri agwa pansi limodzi.”
Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za kubwera kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kudzathira nkhondo Igupto ndi uwu:
“Mulengeze ku Igupto. Mulengeze ku Migidoli.
Mulengezenso ku Mefisi ndi ku Tapanesi.
Muwawuze anthu akumeneko kuti, ‘Imani pamalo panu ndi kukhala okonzeka kudziteteza,
chifukwa lupanga lidzawononga zonse zimene muli nazo.’
Chifukwa chiyani mulungu wanu wamphamvu uja Apisi wathawa?
Iye sakanatha kulimba chifukwa Yehova anamugwetsa.
Ankhondo anu apunthwa ndi kugwa.
Aliyense akuwuza mnzake kuti,
‘Tiyeni tibwerere kwathu,
ku dziko kumene tinabadwira,
tithawe lupanga la adani athu.’
Kumeneku iwo adzafuwula kuti,
‘Farao, mfumu ya ku Igupto mupatseni dzina lakuti,
Waphokoso, Wotaya mwayi wake.’
“Pali Ine wamoyo,” ikutero Mfumu,
imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse,
“wina adzabwera amene ali ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena,
ngati phiri la Karimeli loti njoo mʼmbali mwa nyanja.
Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo
inu anthu a ku Igupto,
pakuti Mefisi adzasanduka chipululu
ndipo adzakhala bwinja mopanda wokhalamo.
“Igupto ali ngati mwana wangʼombe wokongola,
koma chimphanga chikubwera
kuchokera kumpoto kudzalimbana naye.
Ngakhale ankhondo aganyu amene ali naye
ali ngati ana angʼombe onenepa.
Nawonso abwerera mʼmbuyo, nathawa pamodzi.
Palibe amene wachirimika.
Ndithu, tsiku la tsoka lawafikira;
ndiyo nthawi yowalanga.
Aigupto akuthawa ndi liwu lawo lili ngati la njoka yothawa
pamene adani abwera ndi zida zawo,
abwera ndi nkhwangwa
ngati anthu odula mitengo.
Iwo adzadula nkhalango ya Igupto,”
akutero Yehova,
“ngakhale kuti ndi yowirira.
Anthuwo ndi ochuluka kupambana dzombe,
moti sangatheke kuwerengeka.
Anthu a ku Igupto achita manyazi
atengedwa ukapolo ndi anthu a kumpoto.”
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena kuti, “Ndili pafupi kulanga Amoni mulungu wa Tebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Igupto pamodzi ndi milungu yake yonse, mafumu ake ndi onse amene amamukhulupirira. Ndidzawapereka kwa amene akufuna kuwapha, ndiye kuti kwa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni ndi atsogoleri ake ankhondo. Komabe, mʼtsogolomo Igupto adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Yehova.
“Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha;
usataye mtima, iwe Israeli.
Ndithu Ine ndidzakupulumutsa kuchokera ku mayiko akutali,
ndidzapulumutsanso zidzukulu zako kuchokera ku mayiko kumene anapita nazo ku ukapolo.
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala motakasuka ndi pa mtendere,
ndipo palibenso wina amene adzamuopsa.
Iwe mtumiki wanga Yakobo, usachite mantha,
pakuti Ine ndili nawe,” akutero Yehova.
“Ndidzawonongeratu mitundu yonse ya anthu
a ku mayiko kumene ndakupirikitsira,
Koma iwe sindidzakuwononga kotheratu.
Ndidzakulanga iwe ndithu koma moyenerera;
sindidzakulekerera osakulanga.”
Uthenga Wonena za Afilisti
Uthenga umene Yehova anamupatsa mneneri Yeremiya wonena za Afilisti, Farao asanathire nkhondo Gaza ndi uwu:
Yehova akuti,
“Taonani mmene madzi akubwerera kuchokera kumpoto;
adzasanduka mtsinje wosefukira ndi a mkokomo.
Adzasefukira mʼdziko monse ndi kumiza chilichonse mʼmenemo,
mizinda ndi onse okhala mʼmenemo.
Anthu adzafuwula;
anthu onse okhala mʼdzikomo adzalira
akadzamva mgugu wa ngʼombe zazimuna zothamanga,
phokoso la magaleta ake
ndi kulira kwa mikombero yake.
Makolo sadzatembenuka kuti athandize ana awo;
manja awo adzangoti khoba.
Pakuti tsiku lafika
lowononga Afilisti onse
ndi kupha onse otsala,
onse amene akanatha kuthandiza Turo ndi Sidoni.
Yehova ali pafupi kuwononga Afilisti,
otsala ochokera ku zilumba za ku Kafitori.
Anthu a ku Gaza ameta mipala;
anthu a ku Asikeloni akhala chete.
Inu otsala a ku chigwa,
mudzakhala mukudzichekacheka mpaka liti?
“Mukulira kuti, ‘Aa, lupanga la Yehova,
kodi udzapumula liti?
Bwerera mʼmalo ako;
ukhale momwemo ndipo ukhale chete.’
Koma lupangalo lidzapumula bwanji
pamene Yehova walilamulira
kuti lithire nkhondo
Asikeloni ndi anthu a mʼmbali mwa nyanja?”
Uthenga Wonena za Mowabu
Ponena za Mowabu:
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,
“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.
Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;
linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
Palibenso amene akutamanda Mowabu;
ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:
‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’
Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;
ankhondo adzakupirikitsani.
Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.
Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’
Mowabu wawonongeka;
ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.
Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,
akulira kwambiri pamene akupita.
Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka
pa njira yotsikira ku Horonaimu.
Thawani! Dzipulumutseni;
khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.
Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,
nanunso mudzatengedwa ukapolo,
ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.
Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,
ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.
Chigwa chidzasanduka bwinja
ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa
monga Yehova wayankhulira.
Mtsineni khutu Mowabu
chifukwa adzasakazika;
mizinda yake idzasanduka mabwinja,
wopanda munthu wokhalamo.
“Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!
Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!
“Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,
ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,
osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;
iye sanatengedwepo ukapolo.
Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja
ndipo fungo lake silinasinthe.
Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”
akutero Yehova,
“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko
ndipo adzamukhutula;
adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake
pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,
monga momwe Aisraeli anachitira manyazi
ndi Beteli amene ankamukhutulira.
“Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.
Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’
Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;
anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”
ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;
masautso ake akubwera posachedwa.
Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,
inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;
nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,
taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”
“Tsikani pa ulemerero wanu
ndipo khalani pansi powuma,
inu anthu okhala ku Diboni,
pakuti wowononga Mowabu
wabwera kudzamenyana nanu,
wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
Inu amene mumakhala ku Aroeri,
imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.
Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,
afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ”
Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.
Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!
Lengezani ku mtsinje wa Arinoni
kuti Mowabu wawonongedwa.
Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,
ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,
Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,
Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,
Keriyoti ndi Bozira
ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.
Mphamvu za Mowabu zawonongeka;
mkono wake wathyoka,”
akutero Yehova.
“Muledzeretseni Mowabu,
chifukwa anadzikuza powukira Yehova.
Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;
mulekeni akhale chinthu chomachiseka.
Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?
Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba
kuti nthawi zonse poyankhula za iye,
iwe uzimupukusira mutu momunyoza?
Inu amene mumakhala ku Mowabu,
siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.
Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake
pa khomo la phanga.
“Tamva za kunyada kwa Mowabu,
kunyada kwake nʼkwakukulu.
Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.
Ali ndi mtima wodzikweza.
Ine ndikuzidziwa ntchito zake,
akutero Yehova.
Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.
Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,
ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,
ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.
Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.
Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa
imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;
zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.
Wowononga wasakaza
zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
Chimwemwe ndi chisangalalo zatha
ku minda ya zipatso ya ku Mowabu.
Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;
palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.
Ngakhale kufuwula kulipo,
koma sikufuwula kwa chimwemwe.
“A ku Hesiboni ndi Eleali akulira
ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,
kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.
Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu
kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera
ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”
akutero Yehova.
“Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.
Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro
chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
Aliyense wameta mutu wake
ndi ndevu zake;
manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,
ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.
Pa madenga onse a ku Mowabu
ndiponso mʼmisewu yake
anthu akungolira,
pakuti ndaphwanya Mowabu
ngati mtsuko wopanda ntchito,”
akutero Yehova.
“Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!
Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.
Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,
chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”
Yehova akuti,
“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga
chimene chatambalitsa mapiko ake.
Mizinda idzagwidwa
ndipo malinga adzalandidwa.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu
idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu
chifukwa unadzikuza powukira Yehova.
Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira
inu anthu a ku Mowabu,”
akutero Yehova.
“Aliyense wothawa zoopsa
adzagwera mʼdzenje,
aliyense wotuluka mʼdzenje
adzakodwa mu msampha.
Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu
pa nthawi ya chilango chake,”
akutero Yehova.
“Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni
chifukwa chotopa.
Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,
malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.
Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,
dziko la anthu onyada.
Tsoka kwa iwe Mowabu!
Anthu opembedza Kemosi awonongeka.
Ana ako aamuna ndi aakazi
atengedwa ukapolo.
“Komabe masiku akutsogolo
ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”
akutero Yehova.
Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.
Uthenga Wonena za Aamoni
Yehova ananena izi:
Amoni,
“Kodi Israeli alibe ana aamuna?
Kapena alibe mlowamʼmalo?
Tsono nʼchifukwa chiyani anthu opembedza Moleki alanda dziko la Gadi?
Nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Gadi?
Koma nthawi ikubwera,”
akutero Yehova,
“pamene ndidzamveketse mfuwu wankhondo
ku Raba, likulu la Amoni;
ndipo malo awo opembedzera milungu yawo
adzatenthedwa ndi moto.
Choncho Aisraeli adzalandanso dziko lawo
kuchokera kwa amene anawalanda poyamba dzikolo,”
akutero Yehova.
“Lirani, inu anthu a ku Hesiboni chifukwa wowononga uja wafika!
Fuwulani, inu anthu okhala ku Raba!
Valani ziguduli ndi kulira mwamphamvu;
thamangani uku ndi uku mʼkati mwa malinga,
chifukwa mulungu wanu Moleki adzapita ku ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndiponso akuluakulu ake.
Chifukwa chiyani mukunyadira
chigwa chanu,
inu anthu osakhulupirika
amene munadalira chuma chanu nʼkumati:
‘Ndani angandithire nkhondo?’
Ndidzabweretsa zoopsa pa iwe
zochokera kwa onse amene akuzungulira,”
akutero Ambuye, Mulungu Wamphamvuzonse.
“Mudzathawa, ndipo aliyense adzathawitsa moyo wake.
Sipadzapezeka munthu wosonkhanitsanso othawawo.
“Komabe pambuyo pake, ndidzabwezera kwawo Aamoni,”
akutero Yehova.
Uthenga Wonena za Edomu
Yehova Wamphamvuzonse ananena izi za Edomu:
“Kodi nzeru sizikupezekanso ku Temani?
Kodi anzeru analeka kupereka uphungu?
Kodi nzeru zawo zinatheratu?
Inu anthu a ku Dedani, thawani,
bwererani ndi kukabisala ku makwalala
chifukwa ndidzagwetsa mavuto pa zidzukulu za Esau
popeza nthawi yawo ya chiweruzo yafika.
Kodi anthu othyola mphesa akanafika kwa inu
akanakusiyiraniko mphesa pangʼono pokha?
Anthu akuba akanafika usiku
akanangotengako zimene akuzifuna zokha?
Koma ine ndazivula zidzukulu za Esau.
Ndaonetsa poyera malo awo obisalamo,
kotero kuti sadzathanso kubisala.
Ana ake, abale ake pamodzi ndi anansi ake awonongeka.
Palibe wonena kuti,
‘Siyani ana anu amasiye; Ine ndidzawateteza.
Amayi anu amasiye akhoza kudalira Ine.’ ”
Yehova akuti, “Ngati iwo amene sanali oyenera kulangidwa adzamwa chikho cha chiweruzo, ndiye muyesa kuti inuyo simudzalangidwa? Ayi ndithu simudzakhala osalangidwa. Mudzamwa ndithu chikhocho. Ine ndikulumbira, akutero Yehova, kuti mzinda wa Bozira udzasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha, chomachiseka ndiponso chotembereredwa. Mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka muyaya.”
Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova:
Nthumwi yatumidwa kupita kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti,
“Sonkhanani pamodzi kuti muthire nkhondo Edomu!
Konzekerani nkhondo!”
“Ndidzakuchepetsani pakati pa anthu a mitundu ina.
Mudzakhala anthu onyozeka pakati pa anthu.
Kuopseza kwako kwakunyenga;
kudzikuza kwa mtima wako kwakusocheretsa,
iwe amene umakhala mʼmapanga
a mʼmatanthwe ndi mʼmapiri.
Ngakhale utamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,
ndidzakutsitsa pansi kuchokera kumeneko,”
akutero Yehova.
“Dziko la Edomu lidzasanduka chinthu chochititsa mantha.
Onse odutsamo adzadabwa ndi kupukusa mitu yawo
chifukwa cha kuwonongeka kwake.
Monga momwe anawonongekera Sodomu ndi Gomora,
pamodzi ndi mizinda yake yozungulira,”
akutero Yehova,
“motero palibe munthu
amene adzakhala mu Edomu.
“Monga mkango wotuluka ku nkhalango za ku Yorodani
kupita ku malo a msipu wobiriwira,
Ine ndidzapirikitsa anthu a ku Edomu mwadzidzidzi kuchoka mʼdziko lawo.
Pambuyo pake ndidzawayikira owalamulira amene ndamufuna Ine.
Kodi ndani wofanana nane, ndipo angatsutsane nane ndani?
Ndipo ndi mʼbusa uti amene angalimbane nane?”
Nʼchifukwa chake imvani. Izi ndi zimene Ine Yehova
ndakonza zolangira anthu a ku Edomu ndi a ku Temani.
Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo
ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
Akadzagwa Edomu padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera;
kulira kwawo kudzamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.
Taonani, mtundu wina udzachita kuwuluka
nʼkudzatera pa Bozira ngati chiwombankhanga chimene chatambalitsa mapiko ake.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Edomu
idzagunda ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
Uthenga Wonena za Damasiko
Mawu a Yehova onena za Damasiko ndi awa:
“Anthu a ku Hamati ndi a ku Aripadi akuchita mantha
chifukwa amva nkhani yoyipa.
Mitima yawo yagwidwa ndi mantha
ndipo ali ngati muja ichitira nyanja yosakhazikika.
Anthu a ku Damasiko alefuka.
Abwerera mʼmbuyo kufuna kuthawa
chifukwa agwidwa ndi mantha aakulu.
Ali ndi nkhawa komanso mantha
ngati za mayi pa nthawi yake yochira.
Mzinda wotchuka
ndi wachikondwerero uja wasiyidwa!
Nʼchifukwa chake anyamata ake adzagwa mʼmisewu ndi kufa;
ankhondo ake onse adzawonongedwa tsiku limenelo,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Ndidzatentha malinga a Damasiko;
moto udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi.”
Uthenga Wonena za Kedara ndi Hazori
Mawu a Yehova onena za Kedara ndi maufumu a ku Hazori, amene Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anawagonjetsa ndi awa:
“Nyamukani mukathire nkhondo ku Kedara.
Kawonongeni anthu a kummawako.
Landani matenti awo ndi nkhosa zawo,
ndiye kuti, mutenge nsalu zawo ndi katundu wawo.
Mutengenso ngamira zawo.
Anthu adzafuwula kwa iwo kuti,
‘Kuli zoopsa mbali zonse!’
“Thawani mofulumira!
Kabisaleni mʼmakhwawa, inu anthu ku Hazori,”
akutero Yehova.
“Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni wakukonzerani chiwembu;
wakonzekera zoti alimbane nanu.
“Nyamukani kathireni nkhondo mtundu wa anthu umene uli pamtendere,
umene ukukhala mosatekeseka,”
akutero Yehova,
“mzindawo ulibe zipata ngakhalenso mipiringidzo;
anthu ake amakhala pa okha.
Ngamira zawo zidzafunkhidwa,
ndipo makola a ngʼombe zawo adzalandidwa.
Ndidzabalalitsira ku mphepo zinayi onse amene amameta tsitsi lawo chamʼmbali.
Ndidzawagwetsera mavuto kuchokera ku mbali zonse,”
akutero Yehova.
“Hazori adzasanduka bwinja,
malo okhalamo nkhandwe
mpaka muyaya.
Palibe munthu amene adzayendemo.”
Uthenga Wonena za Elamu
Uthenga umene Yehova anapatsa mneneri Yeremiya wonena za Elamu, Zedekiya mfumu ya Yuda atangoyamba kulamulira ndi uwu:
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Taonani, ndidzathyola uta wa Elamu,
umene uli chida chawo champhamvu.
Ndidzabweretsa mphepo zinayi pa Elamu
kuchokera ku zigawo zinayi zamlengalenga;
ndidzawabalalitsira ku mphepo zinayi,
ndipo sipadzakhala dziko
limene anthu a ku Elamu sadzafikako.
A ku Elamuwo ndidzachititsa mantha pamaso pa adani awo
komanso pamaso pa iwo amene akufuna kuwononga moyo wawo.
Ndidzawagwetsera mkwiyo wanga
ndipo adzakhala pa mavuto,”
akutero Yehova.
“Ndidzawapirikitsa ndi lupanga
mpaka nditawatheratu.
Ndidzakhazika mpando wanga waufumu ku Elamu
ndipo ndidzawononga mfumu yake pamodzi ndi akuluakulu ake,”
akutero Yehova.
“Komabe mʼtsogolomo ndidzabwezera
anthu a ku Elamu dziko lawo,”
akutero Yehova.
Uthenga Wonena za Babuloni
Uthenga umene Yehova anayankhula ndi mneneri Yeremiya wonena za mzinda wa Babuloni ndi anthu ake ndi uwu:
“Lengeza ndi kulalika pakati pa anthu a mitundu ina,
kweza mbendera ndipo ulengeze;
usabise kanthu, koma uwawuze kuti,
‘Babuloni wagwa;
mulungu wawo Beli wachititsidwa manyazi,
nayenso Mariduku wagwidwa ndi mantha.
Milungu yake yagwidwa ndi mantha
ndipo mafano ake adzagwidwa ndi mantha.’
Mtundu wa anthu wochokera kumpoto wadzathira nkhondo Babuloni
ndi kusandutsa bwinja dziko lake.
Kumeneko sikudzakhalanso
munthu kapena nyama.
“Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”
akutero Yehova,
“anthu a ku Israeli ndi anthu a ku Yuda
onse pamodzi adzabwera akulira. Adzafunitsitsa kuchita zimene Yehova Mulungu wawo akufuna.
Adzafunsa njira ya ku Ziyoni
ndi kuyamba ulendo wopita kumeneko.
Iwo adzadzipereka kwa Yehova
pochita naye pangano lamuyaya
limene silidzayiwalika.
“Anthu anga ali ngati nkhosa zotayika;
abusa awo
anawasocheretsa mʼmapiri.
Iwo anayendayenda mʼmapiri ndi mʼzitunda
mpaka kuyiwala kwawo.
Aliyense amene anawapeza anawawononga;
adani awo anati, ‘Ife si olakwa,
chifukwa iwo anachimwira Yehova, amene ali mpumulo wawo weniweni
ndi amene makolo awo anamukhulupirira.’
“Thawaniko ku Babuloni;
chokani mʼdziko la Ababuloni.
Muyambe inu kutuluka ngati atonde amene amatsogolera ziweto.
Taonani, ndidzaukitsa gulu lankhondo lamphamvu la mitundu ina
ndi kubwera nalo kuchokera kumpoto
kudzamenyana ndi Babuloni.
Iwo adzandandalika ankhondo awo ndi kugonjetsa Babuloni.
Mivi yawo ili ngati ya ankhondo aluso,
yosapita padera.
Motero Ababuloni adzafunkhidwa;
ndipo onse omufunkha adzakhuta,”
akutero Yehova.
“Inu Ababuloni, munawononga anthu anga osankhika.
Ndiye pano mukukondwa, mukusangalala.
Mukulumphalumpha mokondwa ngati mwana wangʼombe wopuntha tirigu
ndiponso mukulira monyada ngati ngʼombe zazimuna.
Koma mzinda wanu udzachititsidwa manyazi kwambiri.
Mzinda umene uli ngati mayi wanu udzanyazitsidwa.
Babuloni adzasanduka chitsirizira cha anthu onse.
Mzinda wawo udzakhala ngati thengo, ngati dziko lowuma lachipululu.
Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova Babuloni adzakhala wopanda anthu
ndipo adzakhala chipululu chokhachokha.
Onse odutsa kumeneko adzachita mantha ndipo azidzangotsonya
chifukwa cha chiwonongeko chake chachikulu.
“Inu okoka uta,
konzekani kuti muthire nkhondo mzinda wa Babuloni mbali zonse.
Muponyereni mivi yanu yonse
chifukwa anachimwira Yehova.
Mufuwulireni mbali zonse pakuti wagonja.
Nsanja zake zagwa.
Malinga ake agwetsedwa.
Kumeneku ndiko kulipsira kwa Yehova.
Mulipsireni,
mumuchite zomwe iye anachitira anthu ena.
Chotsani ku Babuloni munthu wofesa mbewu aliyense,
ndiponso wodula tirigu ndi chikwakwa chake pa nthawi yokolola.
Poona lupanga la ozunza anzawo,
aliyense adzabwerera kwa anthu ake;
adzathawira ku dziko la kwawo.
“Aisraeli ali ngati nkhosa zomwe zabalalika
pothamangitsidwa ndi mikango.
Mfumu ya ku Asiriya ndiye inayamba kuwapha Aisraeliwo.
Wotsiriza anali Nebukadinezara
mfumu ya ku Babuloni
amene anachita ngati kuphwanya mafupa ake.”
Nʼchifukwa chake Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,
“Ndidzalanga mfumu ya ku Babuloni pamodzi ndi dziko lake
monga momwe ndinalangira mfumu ya ku Asiriya.
Koma ndidzabwezera Israeli ku msipu wake
ndipo adzadya mʼminda ya ku Karimeli ndi Basani;
adzadya nakhuta ku mapiri
a ku Efereimu ndi Giliyadi.
Masiku amenewo, nthawi imeneyo,”
akutero Yehova,
“anthu adzafunafuna zolakwa za Israeli
koma sadzapeza nʼchimodzi chomwe,
ndipo adzafufuza machimo a Yuda,
koma sadzapeza ndi limodzi lomwe,
chifukwa otsala amene ndawasiya ndidzawakhululukira.
“Lithireni nkhondo dziko la Merataimu
ndi anthu okhala ku Pekodi.
Muwaphe ndi lupanga ndi kuwawonongeratu,”
akutero Yehova.
“Chitani zonse monga momwe ndakulamulani.
Mʼdziko muli phokoso la nkhondo,
phokoso la chiwonongeko chachikulu!
Taonani mʼmene waphwanyikira ndi kuwonongekera
uja amati ndi nyundo ya dziko lonse lapansi.
Mzinda wa Babuloni wasanduka chinthu chochititsa mantha
pakati pa mitundu ina!
Ndinakutchera msampha, iwe Babuloni,
ndipo wakodwamo iwe wosazindikira kanthu;
unapezeka ndiponso unakodwa
chifukwa unalimbana ndi Yehova.
Yehova watsekula nyumba ya zida zake
ndipo watulutsa zida za ukali wake,
pakuti Ambuye Yehova Wamphamvuzonse ali ndi ntchito yoti agwire
mʼdziko la Ababuloni.
Mumenyane naye Babuloni mbali zonse.
Anthu ake muwawunjike
ngati milu ya tirigu.
Muwawononge kotheratu
ndipo pasakhale wopulumuka ndi mmodzi yemwe.
Iphani ankhondo ake onse.
Onse aphedwe ndithu.
Tsoka lawagwera
pakuti tsiku lawo lachilango lafika.
Tikumva anthu othawa nkhondo ochokera ku Babuloni
akulengeza mu Yerusalemu
za kulipsira kwa Yehova Mulungu wathu.
Iye akulipsira chifukwa chowononga Nyumba yake.
“Itanani anthu oponya mivi kudzathira nkhondo Babuloni.
Muyitanenso onse amene amakoka mauta.
Mangani misasa ya nkhondo momuzungulira;
musalole munthu aliyense kuthawa.
Muchiteni monga momwe
iye anachitira anthu ena.
Iyeyu ananyoza
Yehova, Woyera wa Israeli.
Nʼchifukwa chake, anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake;
ankhondo ake onse adzaphedwa tsiku limenelo,”
akutero Yehova.
“Taona, ndikukuthira nkhondo, iwe wodzikuzawe,”
akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,
“chifukwa tsiku lako lafika,
nthawi yoti ndikulange yakwana.
Wodzikuzawe udzapunthwa nʼkugwa
ndipo palibe amene adzakudzutse;
ndidzayatsa moto mʼmizinda yake
umene udzanyeketsa onse amene amuzungulira.”
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Anthu a ku Israeli akuzunzidwa,
pamodzi ndi anthu a ku Yuda,
ndipo onse amene anawagwira ukapolo awagwiritsitsa,
akukana kuwamasula.
Koma Mpulumutsi wawo ndi wamphamvu;
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Iye adzawateteza molimba pa mlandu wawo
nʼcholinga choti abweretse mtendere mʼdziko lawo,
koma adzavutitsa okhala ku Babuloni.”
Yehova akuti,
“Imfa yalunjika pa Ababuloni,
pa akuluakulu ake
ndi pa anthu ake a nzeru!
Imfa yalunjika pa aneneri abodza
kuti asanduke zitsiru.
Imfa yalunjika pa ankhondo ake
kuti agwidwe ndi mantha aakulu.
Imfa ilunjike pa akavalo ake ndi magaleta ake.
Ilunjikanso pa magulu ankhondo achilendo amene ali pakati pawo
kuti asanduke ngati akazi.
Chiwonongeko chilunjikenso pa chuma chake
kuti chidzafunkhidwe.
Chilala chilunjike pa madzi ake
kuti aphwe.
Babuloni ndi dziko la mafano,
ndipo anthu afika poyaluka nawo mafanowo.
“Nʼchifukwa chake nyama zakuthengo ndi afisi zidzakhala kumeneko
ndipo kudzakhalanso akadzidzi.
Kumeneko sikudzapezekako anthu,
ndithu anthu sadzakhalako pa mibado yonse.
Monga momwe Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora
pamodzi ndi mizinda yonse yozungulira,”
akutero Yehova,
“momwemonso palibe amene adzakhale kumeneko;
anthu sadzayendanso mʼmenemo.
“Taonani! Gulu lankhondo likubwera kuchokera kumpoto;
mtundu wa anthu amphamvu pamodzi ndi mafumu ambiri,
wanyamuka kuchokera kumathero a dziko lapansi.
Atenga mauta ndi mikondo;
ndi anthu ankhanza ndipo alibe chifundo.
Phokoso lawo likumveka ngati mkokomo wa nyanja.
Akwera pa akavalo awo,
ndipo akonzekera kudzakuthira nkhondo
iwe Babuloni.
Mfumu ya ku Babuloni yamva za mbiri yawo,
ndipo yalobodokeratu.
Ikuda nkhawa,
ikumva ululu ngati wa mayi pa nthawi yake yochira.
Taonani, monga mkango wochokera ku nkhalango ya ku Yorodani
kupita ku msipu wobiriwira,
momwemonso ine ndidzapirikitsa Babuloni mʼdziko lake mwadzidzidzi.
Pambuyo pake ndidzawayikira wowalamulira amene ndamufuna Ine.
Wofanana nane ndani ndipo ndani amene angalimbane nane?
Ndi mtsogoleri wa dziko uti amene anganditengere ku bwalo la milandu?”
Nʼchifukwa chake imvani.
Izi ndi zimene Ine Yehova ndakonza zolangira anthu a ku Babuloni.
Ngakhale ana omwe adzatengedwa ukapolo
ndipo aliyense adzachita mantha chifukwa cha iwo.
Akadzagwa Babuloni padzakhala mfuwu waukulu ndipo dziko lapansi lidzanjenjemera,
ndipo kulira kwawo kudzamveka pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Yehova akuti,
“Taonani, ndidzadzutsa mphepo yowononga
kuti iwononge Babuloni pamodzi ndi anthu a ku Lebi Kamai.
Ndidzatuma alendo ku Babuloni
kudzamupeta ndi kuwononga dziko lake kotheratu.
Iwo adzalimbana naye ku mbali zonse
pa tsiku la masautso ake.
Okoka uta musawalekerere
kapena wonyadira chovala chawo chankhondo.
Musawasiye anyamata ake kuti akhale ndi moyo;
koma muwononge ankhondo ake kotheratu.
Adzavulazidwa ndi kufera mʼdziko la Babuloni
lomwelo ndi mʼmisewu yawo yomwe.
Pakuti Yuda ndi Israeli sanasiyidwe ngati amasiye
ndi Mulungu wawo, Yehova Wamphamvuzonse,
koma ngakhale dziko la Babuloni ndi lodzaza ndi machimo
pamaso pa Woyerayo wa Israeli.
“Thawaniko ku Babuloni!
Aliyense apulumutse moyo wake!
Musawonongeke naye pamodzi chifukwa cha machimo ake.
Imeneyi ndi nthawi yoti Yehova amulange;
Yehova adzamulipsira.
Babuloni anali ngati chikho cha golide mʼdzanja la Yehova;
kuti aledzeretse dziko lonse lapansi.
Mitundu yambiri ya anthu inamwa vinyo wake;
nʼchifukwa chake tsopano inachita misala.
Babuloni wagwa mwadzidzidzi ndi kusweka.
Mulireni!
Mfunireni mankhwala opha ululu wake;
mwina iye nʼkuchira.”
Ena anati, “ ‘Ife tinayesa kumupatsa mankhwala Babuloni,
koma sanachire;
tiyeni timusiye ndipo aliyense apite ku dziko la kwawo,
pakuti mlandu wake wafika mpaka mlengalenga,
wafika mpaka kumwamba.’
“ ‘Yehova waonetsa poyera kuti ndife osalakwa;
tiyeni tilengeze mu Ziyoni
zimene Yehova Mulungu wathu wachita.’
“Yehova wadzutsa mitima ya mafumu a Amedi,
popeza cholinga chake ndi kuwononga Babuloni.
Motero adzalipsira Ababuloni
chifukwa chowononga Nyumba yake.
Ndiye Yehova akuti,
‘Nolani mivi, tengani zishango.’
Kwezani mbendera yankhondo kuti muwononge malinga a Babuloni!
Limbitsani oteteza,
ikani alonda pa malo awo,
konzekerani kulalira.
Pakuti Yehova watsimikiza
ndipo adzachitadi zomwe ananena za anthu a ku Babuloni.
Inu muli ndi mitsinje yambiri
ndi chuma chambiri.
Koma chimaliziro chanu chafika,
moyo wanu watha.
Yehova Wamphamvuzonse analumbira pali Iye mwini kuti:
Ndidzakutumizira adani ochuluka ngati dzombe,
kuti adzakuthire nkhondo ndipo adzafuwula kuonetsa kuti apambana.
“Yehova analenga dziko lapansi ndi mphamvu zake;
Iye anapanga dziko lonse ndi nzeru zake
ndipo anayala thambo mwaluso lake.
Iye akayankhula, kumamveka mkokomo wamadzi akumwamba.
Iyeyo amabweretsa mitambo kuchokera ku malekezero a dziko lapansi.
Amabweretsa mphenzi pamodzi ndi mvula
ndi kutulutsa mphepo yamkuntho kumalo kumene amasungira.
“Anthu onse ndi opusa ndiponso opanda nzeru;
mmisiri aliyense wosula golide akuchita manyazi ndi mafano ake.
Mafano akewo ndi abodza;
alibe moyo mʼkati mwawo.
Mafanowo ndi achabechabe, zinthu zosekedwa nazo.
Pamene anthuwo azidzaweruzidwa mafanowo adzawonongedwa.
Koma Yehova amene ndi Cholowa cha Yakobo sali ngati mafanowo.
Iyeyu ndi Mlengi wa zinthu zonse,
kuphatikizapo mtundu umene anawusankha kuti ukhale anthu ake.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
“Iwe Babuloni ndi ndodo yanga,
chida changa chankhondo.
Ndi iwe ndimaphwanya mitundu ya anthu,
ndi iwe ndimawononga maufumu,
ndi iwe ndimaphwanya kavalo ndi wokwerapo,
ndi iwe ndimaphwanya galeta ndi woyendetsa wake.
Ndi iwe ndimaphwanya mwamuna ndi mkazi,
ndi iwe ndimaphwanya nkhalamba ndi wachinyamata,
ndi iwe ndimaphwanya mnyamata ndi namwali.
Ndi iwe ndimaphwanya mʼbusa ndi ziweto,
ndi iwe ndimaphwanya mlimi ndi ngʼombe,
ndi iwe ndimaphwanya abwanamkubwa ndi atsogoleri a ankhondo.
“Inu mukuona ndidzalanga Babuloni ndi onse amene amakhala mʼdziko la Babuloni chifukwa cha zolakwa zonse anachita ku Ziyoni,” akutero Yehova.
“Taonani, ndikukuzenga mlandu, iwe phiri lowononga,
amene umawononga dziko lonse lapansi,”
akutero Yehova.
“Ndidzatambalitsa dzanja langa pofuna kukulanga,
kukugubuduzira pansi kuchokera pa matanthwe ako,
ndi kukusandutsa kukhala phiri lopserera.
Palibe ngakhale ndi mwala wako umodzi umene anthu adzawutenga
kuti awugwiritse ntchito kumangira nyumba,
chifukwa iwe udzakhala chipululu mpaka muyaya,”
akutero Yehova.
“Kwezani mbendera ya nkhondo mʼdziko!
Lizani lipenga pakati pa mitundu ya anthu!
Konzekeretsani mitundu ya anthu kuti ikamuthire nkhondo;
itanani maufumu awa:
Ararati, Mini ndi Asikenazi kuti adzamuthire nkhondo.
Ikani mtsogoleri wankhondo kuti amenyane naye;
tumizani akavalo ochuluka ngati magulu a dzombe.
Konzekeretsani mitundu ya anthu.
Amenewa ndiwo mafumu a Amedi,
abwanamkubwa awo, atsogoleri a ankhondo,
ndiponso ankhondo a mayiko amene amawalamulira, kuti idzathire nkhondo Babuloni.
Dziko likunjenjemera ndi kunthunthumira,
chifukwa zidzachitikadi zimene Yehova wakonzera Babuloni;
kusakaza dziko la Babuloni
kuti musapezeke wokhalamo.
Ankhondo a ku Babuloni aleka kuchita nkhondo;
iwo angokhala mʼmalinga awo.
Mphamvu zawo zatheratu;
ndipo akhala ngati akazi.
Malo ake wokhala atenthedwa;
mipiringidzo ya zipata zake yathyoka.
Othamanga akungopezanapezana,
amithenga akungotsatanatsatana
kudzawuza mfumu ya ku Babuloni
kuti alande mzinda wake wonse.
Madooko onse alandidwa,
malo onse obisalamo alonda atenthedwa ndi moto,
ndipo ankhondo onse asokonezeka.”
Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,
“Babuloni wokongola uja wakhala ngati malo opunthirapo tirigu
pa nthawi yake yopuntha tirigu; A ku Yerusalemu akuti,
Posachedwapa nthawi yake yomukolola ifika.”
A ku Yerusalemu akuti, “Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni watiwononga,
watiphwanya,
ndi kutitaya ngati mbiya yopanda kanthu.
Watimeza ngati ngʼona,
wakhuta ndi zakudya zathu zokoma,
kenaka nʼkutilavula.”
Anthu a ku Ziyoni anene kuti,
“Zankhanza zimene anatichitira ife ziwabwerere Ababuloni.”
Anthu okhala mu Yerusalemu anene kuti,
“Magazi athu amene anakhetsedwa akhale pa amene akukhala ku Babuloni.”
Nʼchifukwa chake Yehova akuti,
“Taona, ndidzakumenyera nkhondo
ndi kukulipsirira;
ndidzawumitsa nyanja yake
ndipo akasupe ake adzaphwa.
Motero Babuloni adzasanduka mulu wa nyumba zogumuka,
malo okhala nkhandwe,
malo ochititsa mantha ndi onyozedwa,
malo wopanda aliyense wokhalamo.
Anthu ake onse adzabangula ngati mkango,
adzadzuma ngati ana amkango.
Ngati achita dyera
ndiye ndidzawakonzera madyerero
ndi kuwaledzeretsa,
kotero kuti adzasangalala,
kenaka nʼkugona tulo mpaka muyaya ndipo sadzadzukanso,”
akutero Yehova.
“Ine ndidzawatenga
kuti akaphedwe ngati ana ankhosa onenepa,
ngati nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
“Ndithu Babuloni walandidwa,
mzinda umene dziko lonse lapansi limanyadira wagwidwa!
Taonani, mmene Babuloni wasandukira chinthu chochititsa mantha
pakati pa mitundu ya anthu!
Nyanja yakwera ndi kumiza Babuloni;
mafunde ake okokoma aphimba Babuloni.
Mizinda yake yasanduka bwinja,
dziko lowuma ndi lachipululu,
dziko losakhalamo wina aliyense,
dziko losayendamo munthu aliyense.
Ndidzalanga Beli mulungu wa Ababuloni,
ndidzamusanzitsa zimene anameza.
Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye.
Malinga a Babuloni agwa.
“Tulukani mʼBabuloni anthu anga!
Pulumutsani miyoyo yanu!
Thawani mkwiyo woopsa wa Yehova.
Musataye mtima kapena kuchita mantha
pamene mphekesera zikumveka mʼdziko mwanu.
Chaka ndi chaka pamabuka mphekesera
za ziwawa mʼdziko lapansi,
ndiponso yakuti mfumu yakuti ikuthira nkhondo mfumu ina.
Pakuti taonani, nthawi ikubwera ndithu
pamene ndidzalanga mafano a ku Babuloni;
dziko lake lonse lidzachita manyazi
ndi ophedwa ake onse adzakhala ngundangunda pakati pake.
Pamenepo kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo
zidzayimba mokondwa chifukwa cha kugwa kwa Babuloni.
Anthu owononga ochokera kumpoto
adzamuthira nkhondo,”
akutero Yehova.
“Babuloni anapha anthu ambiri pa dziko lapansi.
Tsono, nawo anthu a ku Babuloni ayenera kuphedwa
chifukwa anapha anthu a ku Yerusalemu.
Inu amene munapulumuka ku nkhondo ya Babuloni,
chokani pano ndipo musazengereze!
Kumbukirani Yehova ngakhale muli ku mayiko akutali,
ganizirani za Yerusalemu.”
Inu mukuti, “Tikuchita manyazi,
chifukwa tanyozedwa
ndipo nkhope zathu zili ndi manyazi,
chifukwa anthu achilendo alowa
malo opatulika a Nyumba ya Yehova.”
Nʼchifukwa chake Yehova akuti,
“Masiku akubwera pamene ndidzalanga mafano ake,
ndipo mʼdziko lake lonse
anthu ovulala adzabuwula.
Ngakhale Babuloni atadzikweza mpaka mlengalenga
ndi kulimbitsa nsanja zake,
ndidzatuma anthu owononga kudzamenyana naye,”
akutero Yehova.
“Imvani mfuwu wolira kuchokera ku Babuloni.
Imvani phokoso lachiwonongeko chachikulu
kuchokera mʼdziko la Babuloni.
Pakuti Yehova akuwononga Babuloni,
ndipo akuthetsa phokoso lake lalikulu.
Mfuwu wa adani ukumveka ngati mkokomo wa madzi ambiri.
Phokoso lawo likunka likwererakwerera.
Pakuti wowononga wafika kudzamenyana ndi Babuloni,
ankhondo ake agwidwa,
ndipo mauta awo athyoka.
Paja Yehova ndi Mulungu wobwezera chilango;
adzabwezera kwathunthu.
Ndidzaledzeretsa akuluakulu ake pamodzi ndi anzeru ake,
abwanamkubwa ake, atsogoleri a ankhondo pamodzinso ndi ankhondo;
adzagona kwamuyaya osadzukanso,”
akutero Mfumu, amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Malinga aakulu a Babuloni adzasalazidwa
ndipo zipata zake zazitali zidzatenthedwa;
mitundu ya anthu inangogwira ntchito pachabe.
Anthu anatopa ndi kumanga zimene tsopano zikupsa ndi moto.”
Zedekiya mfumu ya Yuda inali ndi phungu wake wamkulu amene dzina lake linali Seraya mwana wa Neriya chidzukulu cha Maseya. Mʼchaka chachinayi cha ulamuliro wake, Zedekiya anapita ndi Seraya ku Babuloni. Tsono mneneri Yeremiya anamupatsirako uthenga Serayayo. Yeremiya anali atalemba mʼbuku za masautso onse amene adzafike pa Babuloni ndi zina zonse zokhudza Babuloni. Yeremiya anawuza Seraya kuti, “Ukakafika ku Babuloni, ukaonetsetse kuti wawawerengera anthu onse mawu onsewa. Ndipo ukanene kuti, ‘Inu Yehova, mwanena kuti mudzawononga malo ano, kotero kuti simudzatsala munthu kapena nyama mʼdziko muno; lidzakhala chipululu mpaka muyaya.’ Ukakatha kuwerenga bukuli, ukalimangirire ku mwala ndipo ukaliponye pakati pa mtsinje wa Yufurate. Ndipo ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene adzamirire Babuloni ndipo sadzadzukanso chifukwa cha masautso amene adzamugwere.’ ”
Mawu a Yeremiya athera pamenepa.
Kuwonongeka kwa Yerusalemu
Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Yehoyakimu. Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake.
Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni.
Choncho mʼchaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku la khumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo Yerusalemu. Anamanga misasa ndi mitumbira yankhondo kunja kuzungulira mzindawo. Mzindawo unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya.
Pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti munalibe chakudya choti anthu nʼkudya. Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba, koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika.
Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati, kumene anagamula mlandu wake. Ku Ribulako mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona; ndiponso inapha akuluakulu onse a ku Yuda. Ndipo inamukolowola maso Zedekiya, ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni kumene inakamuyika mʼndende kuti akhalemo moyo wake wonse.
Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. Ndipo anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse. Tsono gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene linali ndi mtsogoleri wa ankhondo a mfumu uja linagwetsa malinga onse ozungulira Yerusalemu. Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Komabe Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anasiya anthu ena onse osaukitsitsa a mʼdzikomo kuti azigwira ntchito mʼminda ya mpesa ndi minda ina.
Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni. Ankhondowo anatenganso mbiya, zochotsera phulusa, zozimitsira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho pamodzi ndi ziwiya zina zonse za mkuwa zimene ankagwiritsira ntchito mʼNyumba ya Yehova. Nebuzaradani uja anatenganso mabeseni, ziwiya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoyikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho ndi zina zonse zagolide ndi siliva.
Nsanamira ziwiri zija, chimbiya, maphaka ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri za mkuwa zochirikizira chimbiyacho zimene mfumu Solomoni anapangira Nyumba ya Yehova kulemera kwake kunali kosawerengeka. Nsanamira imodzi kutalika kwake kunali mamita asanu ndi atatu, akazunguliza chingwe inali mamita asanu ndi theka; mʼkati mwake munali bowo ndipo kuchindikala kwake kunali zala zinayi. Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija. Mʼmbali mwake munali makangadza 96; makangadza onse pamodzi analipo 100 kuzungulira ukonde onse.
Mtsogoleri wa ankhondo uja, anagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apachipata. Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo. Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondoyo anawatenga onse napita nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula. Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloniyo inalamula kuti anthuwo aphedwe.
Motero anthu a ku Yuda anapita ku ukapolo, kutali ndi dziko lawo. Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi:
Mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023;
mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,
anatenga anthu 832 kuchokera mu Yerusalemu;
mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,
Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo.
Onse pamodzi analipo anthu 4,600.
Kumasulidwa kwa Yehoyakini
Mʼchaka chimene Evili-Merodaki analowa ufumu wa Babuloni, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, namutulutsa mʼndende. Izi zinachitika pa tsiku la 25 la mwezi wa khumi ndi chiwiri zitatha zaka 37 chitengedwere Yehoyakimu ku ukapolo. Evili-Merodaki anakomera mtima Yehoyakini, namupatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babuloni. Choncho Yehoyakini analoledwa kuvula zovala zake za ku ndende ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse. Tsiku ndi tsiku mfumu ya ku Babuloni inkamupatsa Yehoyakini phoso lake nthawi yonse ya moyo wake, mpaka pa nthawi ya imfa yake.