- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 OWERUZA Oweruza Oweruza Owe Oweruza Aisraeli Achita Nkhondo ndi Akanaani Otsala Atamwalira Yoswa Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Ndani mwa ife ayambe nkhondo yomenyana ndi Akanaani?” Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe kupita. Ndawapatsa dzikolo mʼmanja mwawo.” Choncho Ayuda anawuza abale awo a fuko la Simeoni kuti, “Bwerani tipitire limodzi mʼdziko limene tapatsidwa kuti tikamenyane ndi Akanaani. Ifenso tidzapita nanu mʼdziko limene anakugawirani.” Ndipo Asimeoni anapita nawo. Choncho Ayuda ananyamuka, ndipo Yehova anapereka Akanaani ndi Aperezi mʼmanja mwawo. Ndipo anapha anthu 10,000 ku Bezeki. Ku Bezekiko anakumana ndi ankhondo a mfumu Adoni-Bezeki ndipo anamenyana nawo, ndipo Ayudawo anagonjetsa Akanaani ndi Aperezi. Adoni-Bezekiyo anathawa, koma anamuthamangira ndi kumupeza, namugwira. Atamugwira anamudula zala zake zazikulu za ku manja ndi miyendo. Tsono Adoni-Bezeki anati, “Mafumu 70 omwe anadulidwa zala zazikulu za ku manja ndi miyendo yawo ankatola nyenyeswa pansi pa tebulo langa. Mulungu tsopano wandibwezera zomwe ndinawachita.” Kenaka anapita naye ku Yerusalemu ndipo anafera komweko. Pambuyo pake Ayuda anakathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu ndipo anawulanda. Anapha anthu ambiri ndi kutentha mzinda wonse. Kenaka Ayuda anapita kukamenyana ndi Akanaani omwe amakhala ku dziko la ku mapiri, dziko la Negevi kummwera ndiponso mu zigwa. Anakalimbananso ndi Akanaani amene ankakhala ku Hebroni (mzinda womwe kale unkatchedwa Kiriyati-Araba). Kumeneko anagonjetsa Sesai, Ahimani ndi Talimai. Kuchokera kumeneko, iwo anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” Otanieli mwana wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake. Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani?” Iye anayankha kuti, “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi. Tsono zidzukulu za Hobabu, Mkeni uja, mpongozi wa Mose, zinachoka ku Yeriko mzinda wa migwalangwa pamodzi ndi anthu a fuko la Yuda mpaka ku chipululu chimene chili kummwera kwa Aradi ndi kukakhala ndi Aamaleki. Kenaka anthu a fuko la Yuda anapita pamodzi ndi abale awo a fuko la Simeoni ndi kukagonjetsa Akanaani amene amakhala ku Zefati, ndipo mzindawo anawuwononga kwambiri. Choncho mzindawo anawutcha Horima. Anthu a fuko la Yuda analandanso mzinda wa Gaza ndi dziko lonse lozungulira, mzinda wa Asikeloni pamodzi ndi dziko lake lonse lozungulira, ndi mzinda wa Ekroni pamodzi ndi dziko lonse lozungulira. Yehova anathandiza anthu a fuko la Yuda. Iwo analanda dziko la kumapiri, koma sanathe kuwachotsa anthu ku zigwa, chifukwa anali ndi magaleta azitsulo. Monga analonjezera Mose, Kalebe anapatsidwa Hebroni. Kalebe anapirikitsa mafuko atatu a Anaki mu mzindamo. Koma fuko la Benjamini linalephera kuwachotsa Ayebusi, amene amakhala mu Yerusalemu. Choncho Ayebusiwo akukhalabe ndi fuko la Benjamini mu Yerusalemu mpaka lero. A banja la Yosefe nawonso anathira nkhondo mzinda wa Beteli, ndipo Yehova anali nawo. Anatumiza anthu kuti akazonde Beteli. Mzindawo kale unkatchedwa Luzi. Anthu okazondawo anaona munthu akutuluka mu mzindamo ndipo anamuwuza kuti, “Tisonyeze njira yolowera mu mzindamu, ndipo ife tidzakuchitira chifundo.” Choncho iye anawaonetsa njirayo, ndipo iwo anapha anthu onse mu mzindamo ndi lupanga koma munthu uja pamodzi ndi banja lake sanawaphe. Ndipo iye anapita ku dziko la Ahiti, kumene anamangako mzinda nawutcha dzina lake Luzi. Mpaka lero lino mzindawo dzina lake ndi lomwelo. Koma a fuko la Manase sanachotse nzika za mzinda wa Beti-Seani pamodzi ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena nzika za mzinda wa Taanaki ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapenanso nzika za mzinda wa Dori ndi mʼmidzi yake yozungulira. Iwo sanapirikitse nzika za mzinda wa Ibuleamu ndi mʼmidzi yake yozungulira, kapena mzinda wa Megido ndi mʼmidzi yake yozungulira. Choncho Akanaani anapitirirabe kukhala mʼdzikomo. Aisraeli atakhala amphamvu, anawagwiritsa Akanaaniwo ntchito yakalavulagaga, koma sanawapirikitse. Nawonso Aefereimu sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Gezeri, choncho Akanaaniwo ankakhalabe pakati pawo ku Gezeriko. Azebuloni sanathamangitse Akanaani amene amakhala mu Kitironi kapena a ku Nahaloli. Iwo ankakhala pakati pawo ndipo ankawagwiritsa ntchito yakalavulagaga. A fuko la Aseri nawo sanathamangitse amene amakhala mu Ako, Sidoni, Ahilabu, Akizibu, Heliba, Afiki, ndi Rehobu. Choncho anthu a fuko la Aseri anakhala pakati pa Akanaani amene ankakhala mʼdzikomo popeza sanawapirikitse. Nalonso fuko la Nafutali silinathamangitse anthu amene ankakhala ku Beti Semesi kapena ku Beti Anati. Koma Anafutaliwo ankakhala pakati pa Akanaaniwo mʼdzikomo. Koma anthu amene ankakhala ku Beti Semesi ndi ku Beti Anati anawasandutsa kukhala ogwira ntchito yathangata. Aamori anapirikitsira anthu a fuko la Dani ku dziko la ku mapiri popeza sanawalole kuti atsikire ku chigwa. Aamori anatsimikiza mtima zokhalabe ku phiri la Hara-Heresi, ku Ayaloni, ndiponso ku Saalibimu. Koma a fuko la Yosefe anakula mphamvu ndipo anagwiritsa Aamoriwo ntchito yakalavulagaga. Malire a Aamori anayambira ku chikweza cha Akirabimu nʼkulowera ku Sela napitirira kumapita chakumapiri ndithu. Mngelo wa Yehova ku Bokimu Mngelo wa Yehova anapita ku Bokimu kuchokera ku Giligala ndipo anati kwa Aisraeli, “Ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndikukulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo anu. Ndinati ‘Sindidzaswa pangano langa ndi inu, ndipo inu musadzachite pangano ndi anthu a dziko lino, koma mudzaphwanye maguwa awo ansembe.’ Koma inu simunamvere lamulo langa. Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? Ndikukuwuzani tsopano kuti sindithamangitsa nzikazo pamene inu mukufika. Ndidzawasandutsa kukhala adani anu ndipo milungu yawo idzakhala ngati msampha kwa inu.” Mngelo wa Mulungu atayankhula izi kwa Aisraeli, onse analira mokweza, ndipo anatcha malowo kuti Bokimu (kutanthauza kuti Olira). Pamenepo anapereka nsembe kwa Yehova. Agonjetsedwa Chifukwa Chosamvera Yoswa atawuza Aisraeli kuti achoke, iwo anapita kukatenga dzikolo, aliyense dera lake. Anthuwo anatumikira Yehova masiku onse a moyo wa Yoswa. Atamwalira Yoswa, Aisraeli anatumikirabe Yehova nthawi yonse ya moyo wa akuluakulu amene anaona zazikulu zimene Yehova anawachitira. Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Yehova, anamwalira ali ndi zaka 110. Ndipo anamuyika mʼmanda a mʼdziko lake, ku Timnati-Heresi mʼdziko la mapiri la Efereimu, kumpoto kwa phiri la Gaasi. Mʼbado onse utapita kukakhala ndi anthu a mtundu awo, kenaka panauka mʼbado wina umene sunadziwe Yehova ngakhale ntchito zazikulu zimene Yehova anachitira Aisraeli. Choncho Aisraeli anayamba kuchita zinthu zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anatumikira Abaala. Iwo anasiya Yehova Mulungu wa makolo awo, amene anawatulutsa ku Igupto. Ndipo anatsatira ndi kupembedza milungu yosiyanasiyana ya anthu amene anawazungulira. Motero Aisraeli anakwiyitsa Yehova. Iwo anasiya Yehova ndi kumatumikira Baala ndi Asiteroti. Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha amene ankasakaza zinthu zawo. Ndipo analola kuti adani awo owazungulira amene sanathenso kulimbana nawo, awagonjetse. Nthawi zonse Aisraeli ankati akapita ku nkhondo, Yehova amalimbana nawo kuti agonjetsedwe, monga ananenera molumbira kuti zidzaterodi. Choncho iwo anali pa mavuto aakulu. Choncho Yehova anawawutsira atsogoleri amene ankawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankasakaza zinthu zawo. Komabe iwo sanawamvere atsogoleri awowo popeza ankapembedza milungu ina ndi kumayigwadira. Iwo anapatuka msangamsanga mu njira imene ankayendamo makolo awo. Iwo aja ankamvera malamulo a Yehova, koma mʼbado uwu ayi. Nthawi zonse Yehova akawautsira mtsogoleri, Iye amakhala naye, ndipo mtsogoleriyo ankawapulumutsa Aisraeliwo mʼmanja mwa adani awo mʼnthawi imene anali moyo. Yehova ankawamvera chisoni Aisraeli pamene ankabuwula chifukwa cha anthu owazunza ndi kuwasautsa. Koma nthawi zonse mtsogoleri akamwalira, Aisraeli ankabwerera mʼmbuyo. Iwo amadzisandutsa oyipa kupambana makolo awo popeza ankatsata milungu ina, kuyitumikira ndi kumayigwadira. Anakana kusiya makhalidwe awo oyipa ndi njira zawo zamakani. Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeli ndipo anati, “Chifukwa mtundu uwu waswa pangano limene ndinakhazikitsa ndi makolo awo ndipo sanandimvere, Inenso sindidzapirikitsanso mtundu uli wonse wa anthu amene Yoswa anawasiya pomwalira. Ndidzatero kuti ndiwayese Aisraeli ndi kuona ngati adzasamala kuyenda mʼnjira ya Ine Yehova monga momwe ankachitira makolo awo.” Choncho Yehova anayileka mitundu imeneyi ndipo sanayithamangitse kapena kuyipereka mʼmanja mwa Yoswa. Iyi ndi mitundu ya anthu yomwe Yehova anayisiya kuti ayese nayo Aisraeli amene sanadziwe kumenya nkhondo mu Kanaani (Yehova anachita izi kuti Aisraeli onse aphunzire kumenya nkhondo; makamaka amene nʼkale lonse sanadziwe kumenya nkhondo. Mitundu ya anthuyo ndi: Mafumu asanu a Afilisti, Akanaani onse, Asidoni, ndi Ahivi amene ankakhala ku mapiri a Lebanoni kuyambira ku phiri la Baala-Herimoni mpaka ku Lebo Hamati. Iwowa Yehova anawasiya kuti aziyesa nawo Aisraeli kuti aone ngati angamvere malamulo a Yehova, amene anapatsa makolo awo kudzera mwa Mose. Choncho Aisraeli anakhala pakati pa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Tsono Aisraeli aja amalola ana awo aamuna ndi aakazi kuti azikwatira ndi kukwatiwa ndi anthu amitundu ina. Kenaka anayamba kupembedza milungu yawo. Otanieli Aisraeli anachita zinthu zoyipira Yehova. Iwowa anayiwala Yehova Mulungu wawo ndi kumatumikira Abaala ndi Asera. Choncho Yehova anawapsera mtima Aisraeliwo ndipo anawagulitsa kwa Kusani-Risataimu mfumu ya ku Mesopotamiya. Choncho Aisraeli anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zisanu ndi zitatu. Koma pamene Aisraeliwo analirira kwa Yehova, Iye anawawutsira mpulumutsi, Otanieli mwana wamwamuna wa Kenazi, mngʼono wake wa Kalebe. Iyeyu ndiye anawapulumutsa. Mzimu wa Yehova unatsika pa iye, choncho anasanduka mtsogoleri wa Israeli. Iye anapita kukamenya nkhondo, ndipo Yehova anapereka Kusani-Risataimu mfumu ya Aaramu mʼmanja mwake. Choncho anayigonjetsa. Ndipo mʼdzikomo munakhala mtendere zaka makumi anayi. Kenaka Otanieli mwana wa Kenazi anamwalira. Ehudi Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Tsono Yehova anapatsa mphamvu Egiloni, mfumu ya Mowabu kuti alimbane ndi Aisraeli aja popeza anachita zinthu zoyipira Yehova. Egiloniyo anamemeza Aamori ndi Aamaleki kupita kukamenyana ndi Israeli, ndipo analanda Yeriko, mzinda wa migwalangwa. Aisraeli anatumikira ngati akapolo Egiloni mfumu ya Mowabu kwa zaka 18. Aisraeli analiranso kwa Yehova, ndipo Iye anawawutsira mpulumutsi, Ehudi. Iyeyu anali mwana wa Gera, munthu wamanzere, wa fuko la Benjamini. Aisraeli ankatumiza msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, kudzera kwa Ehudi. Ndipo Ehudi anapanga lupanga lakuthwa kuwiri lotalika masentimita makumi asanu, ndipo anamangirira lupangalo pa ntchafu yake ya kumanja mʼkati mwa zovala zake. Iye anakapereka msonkho kwa Egiloni, mfumu ya Mowabu, amene anali munthu wonenepa kwambiri. Ehudi atapereka msonkhowo, anawuza anthu amene ananyamula msonkhowo kuti azipita. Iye mwini anabwerera pamalo a miyala yozokotedwa ku Giligala ndipo anati, “Zikomo mfumu, ine ndili ndi mawu achinsinsi kuti ndikuwuzeni.” Mfumuyo inawuza onse amene amayitumikira kuti akhale chete, ndipo kenaka anawatulutsa. Kenaka Ehudi anayandikira pafupi ndi mfumuyo, ndipo iyo inakhala yokha mʼchipinda chapamwamba, mozizira bwino. Tsono Ehudi anati, “Ndili ndi mawu ochokera kwa Mulungu woti ndikuwuzeni.” Mfumuyo itadzuka pa mpando wake waufumu, Ehudi ndi dzanja lake lamanzere, anasolola lupanga pa ntchafu yake ya kumanja ndi kubaya nalo mfumuyo pa mimba. Lupanga linalowa mʼmimba pamodzi ndi chogwirira chake. Mafuta anaphimba lupangalo popeza silinatulutsidwe mʼmimbamo. Ndiponso matumbo anatuluka. Kenaka Ehudi anatuluka panja pa khonde, atatseka ndi kukhoma zitseko za chipinda chapamwambacho. Ehudi atachoka, atumiki a mfumu aja anabwera, ndipo ataona kuti zitseko za chipinda chapamwamba zinali zokhoma anaganiza kuti mwina mfumu ikudzithandiza mʼkatimo. Iwo anadikira nthawi yayitali koma popanda chochitika. Koma ataona kuti mfumuyo sikutsekulabe zitseko za chipindacho, iwo anatenga makiyi ndi kutsekula zitsekozo, ndipo anangoona mbuye wawo atagwera pansi, ali wakufa. Ehudi anathawa pamene iwo ankadikira. Iye anadzera ku malo a miyala yozokotedwa kuja ndi kuthawa kupita ku Seiri. Atafika kumeneko, anayimba lipenga ku dziko la ku mapiri la Efereimu. Iye akutsogolera, Aisraeli onse anatsika naye pamodzi kuchoka ku mapiriko. Iye anawawuza kuti, “Nditsatireni, chifukwa Yehova wapereka Amowabu, adani anu mʼmanja mwanu.” Choncho anthuwo anamutsatira, nalanda madooko a Yorodani opita ku Mowabu. Iwo sanalole kuti wina aliyense awoloke. Nthawi imeneyo anapha Amowabu pafupifupi 10,000. Ophedwawo anali anthu amphamvu komanso odziwa kumenya nkhondo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anathawa. Tsiku limenelo Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Israeli, ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 80. Samugara Ehudi atamwalira, panabwera Samugara mwana wa Anati. Iye anapha Afilisti 600 ndi ndodo yomenyera ngʼombe. Nayenso anapulumutsa Israeli. Debora Ehudi atamwalira, Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova. Choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Yabini, mfumu ya ku Kanaani, imene inkalamulira ku Hazori. Mkulu wa ankhondo ake anali Sisera, amene ankakhala ku Haroseti-Hagoyimu. Aisraeli analira kwa Yehova kuti awathandize, chifukwa Sisera anali ndi magaleta achitsulo 900 ndipo anazunza Aisraeli mwankhanza kwa zaka makumi awiri. Debora, mneneri wamkazi, mkazi wake wa Rapidoti ndiye ankatsogolera Israeli nthawi imeneyo. Iye ankakhala pansi pa mtengo wa mgwalangwa wa Debora, pakati pa Rama ndi Beteli mʼdziko la ku mapiri la Efereimu, ndipo Aisraeli ankapita kwa iye kuti akaweruze milandu yawo. Debora uja anatuma munthu kuti akayitane Baraki mwana wa Abinoamu wa ku Kedesi mʼdziko la Nafutali ndipo anati kwa iye, “Yehova Mulungu wa Israeli akukulamula iwe kuti, ‘Pita kasonkhanitse anthu ku phiri la Tabori. Ubwere nawo anthu 10,000 a fuko la Nafutali ndi a fuko la Zebuloni. Ine ndidzakokera Sisera mkulu wa ankhondo a Yabini pamodzi ndi magaleta ake ndi asilikali ake kwa inu ku mtsinje wa Kisoni ndipo ndidzamupereka mʼmanja mwanu.’ ” Baraki anamuyankha kuti, “Mukapita nane limodzi ine ndipita. Koma ngati sitipitira limodzi, inenso sindipita.” Debora anati, “Chabwino, ine ndipita nawe limodzi. Koma mudziwe kuti inu simudzalandirapo ulemu pa zimene mwachitazi popeza Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwa munthu wamkazi.” Choncho Debora ananyamuka kupita ku Kedesi pamodzi ndi Baraki. Baraki anayitana mafuko a Zebuloni ndi Nafutali kuti abwere ku Kedesi. Anthu 10,000 anamutsatira, ndipo Debora anapita naye pamodzi. Nthawi imeneyo nʼkuti Mkeni wina dzina lake Heberi atalekana ndi Akeni anzake, zidzukulu za Hobabu, mlamu wa Mose, nakamanga tenti yake pafupi ndi mtengo wa thundu ku Zananimu pafupi ndi Kedesi. Pamene Sisera anamva kuti Baraki mwana wa Abinoamu wapita ku phiri la Tabori, anasonkhanitsa magaleta ake achitsulo 900 ndi anthu onse amene anali naye ndipo anachoka ku Haroseti-Hagoyimu kupita ku mtsinje wa Kisoni. Debora anawuza Baraki kuti, “Dzukani! Paja ndi lero limene Yehova wapereka Sisera mʼmanja mwako. Kodi Yehova sanakhale akukutsogolerani?” Choncho Baraki anatsika phiri la Tabori, anthu 10,000 akumutsata. Yehova anasokoneza Sisera ndi magaleta ake pamodzi ndi ankhondo ake onse. Baraki ndi anthu ake anawapirikitsa ndipo Sisera anatsika pa galeta yake nayamba kuthawa pansi. Baraki analondola magaletawo pamodzi ndi ankhondo onse mpaka ku Haroseti-Hagoyimu, ndipo ankhondo onse a Sisera anaphedwa ndi lupanga. Palibe munthu ndi mmodzi yemwe anatsala. Komabe Sisera anathawa pansi mpaka anakafika ku tenti ya Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni uja, chifukwa panali mtendere pakati pa Yabini mfumu ya Hazori ndi banja la Heberi, Mkeni uja. Yaeli anatuluka kukachingamira Sisera ndipo anati, “Bwerani mbuye wanga, lowani momwemo musaope.” Choncho analowa mʼtenti muja, ndipo anamufunditsa chofunda. Anati, “Ndili ndi ludzu, chonde patseniko madzi pangʼono akumwa, ndili ndi ludzu.” Mkaziyo anatsekula thumba la chikopa mmene munali mkaka, namupatsa kuti amwe, ndipo anamufunditsanso. Kenaka anawuza mkaziyo kuti, “Muyime pa khomo la tentili, ndipo munthu wina akabwera kudzakufunsani kuti, ‘Kodi kwafika munthu wina kuno?’ Inu muyankha kuti, ‘Ayi.’ ” Koma Yaeli mkazi wa Heberi, anatenga chikhomo cha tenti ndi hamara ndi kupita mwakachetechete kwa Sisera uja. Tsono Sisera ali mtulo chifukwa chotopa, mkazi uja anamukhomera chikhomo chija mʼmutu mwake. Chinatulukira kwinaku mpaka kulowa mʼnthaka, ndipo anafa pomwepo. Baraki atafika akulondola Sisera, Yaeli anatuluka kukamuchingamira namuwuza kuti, “Lowani mudzaone munthu amene mukumufunafuna.” Tsono atalowa anangoona Sisera ali thapsa pansi wakufa ndi chikhomo chili mʼmutu mwake. “Choncho pa tsiku limenelo Mulungu anagonjetsa Yabini mfumu ya Akanaani, pamaso pa Aisraeli. Ndipo Aisraeli anapanikizabe Yabini, mfumu ya Akanaani, mpaka kumuwonongeratu. Nyimbo ya Debora “Tsiku limenelo Debora ndi Baraki mwana wa Abinoamu anayimba nyimbo iyi: “Popeza kuti atsogoleri anatsogoleradi mʼdziko la Israeli; ndipo anthu anadzipereka okha mwa ufulu, tamandani Yehova: “Imvani inu mafumu! Tcherani khutu, atsogoleri inu! Ndidzayimba nyimbo, ndidzayimbira Yehova, Mulungu wa Israeli nyimbo yokoma. “Inu Yehova, pamene munkatuluka mu Seiri, pamene mumayenda kuchokera mʼdziko la Edomu, dziko linagwedezeka, mitambo inasungunuka nigwetsa madzi. Mapiri anagwedezeka pamaso pa Yehova, Mulungu wa Israeli. “Pa nthawi ya Samugara mwana wa Anati, pa nthawi ya Yaeli, misewu inasiyidwa; alendo ankangoyenda mʼtinjira takumbali. Anthu a ku midzi anathawa; mu Israeli munalibe midzi mpaka pamene iwe Debora unafika; unafika ngati mayi ku Israeli. Pamene anasankha milungu ina, nkhondo inabwera ku zipata za mzinda, ndipo chishango kapena mkondo sizinapezeke pakati pa anthu 40,000 mu Israeli. Mtima wanga uli ndi atsogoleri a Israeli, uli ndi anthu amene anadzipereka okha mwaufulu pakati pa anthu. Tamandani Yehova! “Inu okwera pa abulu oyera, okhala pa zishalo, ndi inu oyenda pa msewu, yankhulani. Ku zitsime, kutali ndi phokoso la a mauta; kumeneko akusimba za kuti Yehova wapambana; akusimba kuti Yehova walipsira anthu ake mu Israeli. “Choncho anthu a Yehova anasonkhana ku zipata za mzinda. Anati, ‘Tsogolera ndiwe, Debora, tsogolera; tsogolera ndiwe, tsogolera, imba nyimbo. Iwe Baraki! nyamuka Tsogolera akapolo ako, iwe mwana wa Abinoamu.’ “Kenaka anthu okhulupirika anatsatira atsogoleri awo; anthu a Yehova anapita kukamenyera Yehova nkhondo kulimbana ndi adani amphamvu. Anakalowa mʼchigwa kuchokera ku Efereimu; akutsatira iwe Benjamini ndi abale ako. Akulu a ankhondo anachokera ku Makiri, ndipo onyamula ndodo ya udindo anachokera ku Zebuloni. Olamulira a Isakara anali pamodzi ndi Debora; inde, anthu ochokera ku Isakara anatsatanso Baraki, ndipo anathamangira ku chigwa akumutsatira. Koma pakati pa mafuko a Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuchita. Chifukwa chiyani munangokhala ku makola a nkhosa nʼkumangomvetsera zitoliro zoyitanira nkhosa? Pakati pa anthu a fuko la Rubeni panali kusinkhasinkha mtima kwambiri osadziwa chenicheni choyenera kuti achite. Agiliyadi anatsala pa tsidya la Yorodani. Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu afuko la Dani anatsarira mʼsitima za pa madzi? Aseri anali pa gombe la Nyanja; anangokhala mʼmadooko mwawo. Azebuloni ndi anthu amene anayika moyo wawo mʼzoopsa. Nawonso anthu a fuko la Nafutali anayika miyoyo yawo pa chiswe pomenya nkhondo pamwamba pa mapiri. “Mafumu anabwera, anachita nkhondo; mafumu Akanaani anachita nkhondo ku Tanaki pafupi ndi madzi a ku Megido, koma sanatengeko zofunkha zasiliva. Ngakhalenso nyenyezi zakumwamba zinachita nkhondo, zinathira nkhondo Sisera, zikuyenda mʼnjira zake. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola, chigumula cha mtsinje wa Kisoni chinawakokolola. Mtima wanga, yenda mwamphamvu, limbika! Ndipo ziboda za ngʼombe zazimuna zinachita phokoso lalikulu, akavalo ali pa liwiro, akuthamanga kwambiri. Mngelo wa Yehova anati ‘Tembererani Merozi.’ ‘Tembererani nzika zake mwaukali, chifukwa sanabwere kudzathandiza Yehova, kulimbana ndi adani ake amphamvu.’ “Akhale wodala kupambana akazi onse, Yaeli mkazi wa Heberi Mkeni; inde mwa akazi onse okhala mʼdziko, akhale wodala iyeyu. Munthu uja anapempha madzi akumwa, koma iye anamupatsa mkaka; anamupatsa chambiko mʼchikho cha wolemekezeka. Anatenga chikhomo cha tenti mʼdzanja lake, anatenganso nyundo ndi dzanja lake lamanja. Ndipo anakhoma nacho Sisera, anamuphwanya mutu wake, ndi kumubowola mu litsipa mwake. Anathifukira ku mapazi a mkaziyo nagwa, anagwa; iye anagona pamenepo. Anagwera pa mapazi a mkaziyo, iye anagwa; pamene anagwera, pamenepo anaferapo. “Amayi ake a Sisera anasuzumira pa zenera; nafuwula mokweza kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani galeta lake lachedwa kufika? Nʼchifukwa chiyani phokoso la magaleta ake silikumveka?’ Amayi ake anzeru kwambiri anamuyankha, ndithudi, mwiniwake anadziyankha yekha kuti, ‘Kodi iwo sakufunafuna zofunkha kuti agawane; akugawana wankhondo aliyense mtsikana mmodzi kapena awiri. Sisera akumupatsa zofunkha: zovala zonyikidwa mu utoto, zoti ndizivala mʼkhosi zovala zopeta zonyika mu utoto, ndi zopeta zomavala mʼkhosi?’ “Choncho Yehova! adani anu onse awonongeke, koma iwo amene amakukondani inu akhale ngati dzuwa pamene lituluka ndi mphamvu zake.” Ndipo dziko linakhala pa mtendere zaka makumi anayi. Gideoni Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, choncho Yehova anawapereka mʼmanja mwa Amidiyani kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Amidiyani anapondereza Aisraeli. Tsono chifukwa cha Amidiyaniwa, Aisraeli anakonza malo obisalamo mʼmapiri ndi mʼmapanga. Anamanganso malinga. Aisraeli amati akadzala mbewu, Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena akummawa amabwera ndi kudzawathira nkhondo. Iwo anamanga misasa mʼdzikomo ndi kuwononga zokolola zawo zonse mpaka ku Gaza, ndipo sanawasiyireko chamoyo chilichonse Aisraeliwo, kaya nkhosa kapena ngʼombe ndi bulu yemwe. Iwo ankabwera ndi zoweta zawo ndi matenti awo omwe. Ankabwera ambiri ngati dzombe, motero kuti kunali kovuta kuwawerenga anthuwo ndi ngamira zawo. Tsono iwo ankabwera ndi kuwononga dziko lonse. Aisraeli anasauka chifukwa cha Amidiyani ndipo analirira kwa Yehova kuti awathandize. Pamene Aisraeli analirira kwa Yehova chifukwa cha Amidiyaniwo, Iye anawatumizira mneneri amene anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndine amene ndinakutsogolerani kuchokera ku Igupto. Ndinakutulutsani mʼdziko la ukapolo. Ine ndinakupulumutsani ku ulamuliro wa Igupto komanso mʼmanja mwa amene amakuzunzani. Ndinawathamangitsa adani anu inu mukufika, ndikukupatsani dziko lawo.’ Ndipo ndinakuwuzani kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu; musapembedze Milungu ya Aamori amene mukukhala mʼdziko lawo.’ Koma inu simunandimvere.” Tsiku lina mngelo wa Yehova anabwera ku Ofura ndi kukhala pansi pa tsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yowasi Mwabiezeri. Tsono Gideoni, mwana wake nʼkuti pa nthawiyo akupuntha tirigu mʼmalo ofinyira mphesa mowabisalira Amidiyani. Tsono mngelo wa Yehova uja anamuonekera Gideoni nati kwa iye, “Yehova ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.” Gideoni anayankha, “Koma mbuye wanga, ngati Yehova ali nafedi, nʼchifukwa chiyani zonsezi zationekera? Nanga ntchito zake zodabwitsa zimene makolo athu anatiwuza pamene anati, ‘Yehova anatitulutsa ku dziko la Igupto,’ zili kuti? Koma tsopano Yehova watitaya ndi kutipereka mʼmanja mwa Amidiyani.” Yehova anamuyangʼana namuwuza kuti, “Pita ndi mphamvu zomwe uli nazo, ukapulumutse Aisraeli mʼmanja mwa Amidiyani. Kodi si ndine amene ndakutuma?” Koma Gideoni anafunsa kuti, “Kodi Ambuye anga ine ndingapulumutse bwanji Israeli? Mbumba yanga ndi yopanda mphamvu mu fuko la Manase, ndiponso ine ndine wamngʼono kwambiri mʼbanja mwa abambo anga.” Yehova anamuyankha kuti, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo Amidiyaniwo udzawagonjetsa ngati munthu mmodzi.” Gideoni anati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, ndionetseni chizindikiro kusonyeza kuti ndinudi mukuyankhula ndi ine. Chonde musachoke msanga mpaka nditabwerera kwa inu ndi chopereka changa cha chakudya kudzachipereka kwa inu.” Ndipo Yehova anamuwuza kuti, “Ine ndikudikira mpaka utabweranso.” Gideoni analowa mʼnyumba, ndipo anakakonza mwana wambuzi, nakonzanso makeke wopanda yisiti a ufa wa makilogalamu khumi. Nayika nyamayo mʼdengu ndipo msuzi wake anawuthira mu mʼphika. Anabwera nazo ndi kukazipereka kwa mngelo uja pa tsinde pa mtengo wa thundu paja. Mngelo wa Mulungu anamuwuza iye kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekewa, uziyike pa mwala uwu ndi kuthirapo msuziwu.” Ndipo Gideoni anatero. Mngelo wa Yehova anatenga msonga ya ndodo imene inali mʼmanja mwake nakhudza nayo nyama ndi makeke aja. Nthawi yomweyo moto unabuka pa thanthwepo ndi kupsereza nyama yonse ndi makeke aja. Ndipo mngelo wa Yehova sanaonekenso. Apo Gideoni anazindikira kuti analidi mngelo wa Ambuye, ndipo anati, “Kalanga ine Yehova Wamphamvuzonse! Ine ndaona mngelo wa Yehova ndi maso!” Koma Yehova anamuwuza kuti, “Mtendere ukhale ndi iwe! Usachite mantha, sufa ayi.” Choncho Gideoni anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo analitcha kuti, Yehova ndiye mtendere. Kufikira lero lino guwali lilipo ku Ofura wa Mwabiezeri. Usiku womwewo Yehova anati kwa Gideoni, “Tenga ngʼombe ya mphongo ya abambo ako, ngʼombe ina yachiwiri ya zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ugwetse guwa la Baala limene abambo ako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pafupi pake. Kenaka umangire Yehova Mulungu wako guwa lansembe ndi miyala yoyala bwino pamwamba pa chiwunda chimenecho. Utenge ngʼombe ya mphongo yachiwiri ija ndipo uyipereke ngati nsembe yopsereza pogwiritsa ntchito mitengo ya fano la Asera imene udule ngati nkhunizo.” Choncho Gideoni anatenga antchito ake khumi nachita monga Yehova anamuwuzira. Ndipo popeza ankaopa anthu a pa banja lake ndiponso anthu a mʼmudzimo sanachite zimenezi masana koma usiku. Anthu a mu mzindamo atadzuka mʼmamawa anangoona guwa la Baala litagwetsedwa ndi fano la Asera limene linali pamwamba pake litadulidwa ndiponso ngʼombe yamphongo yachiwiri ija itaperekedwa ngati nsembe yopsereza pa guwa limene linamangidwa lija. Iwo anafunsana wina ndi mnzake, “Wachita zimenezi ndani?” Atafufuza ndi kufunsafunsa, analingalira kuti, “Gideoni mwana wa Yowasi ndiye wachita zimenezi.” Ndipo anthuwo anawuza Yowasi kuti, “Tulutsa mwana wako, ayenera kufa chifukwa wagumula guwa lansembe la Baala ndipo wadula fano la Asera lomwe linali pamwamba pake.” Koma Yowasi anawuza anthu amene anamuzungulirawo kuti, “Kodi inu mukuti mukhale woyankhulira Baala mlandu? Kodi ndinu amene mukuti mumupulumutse? Amene akufuna kumumenyera nkhondo Baala akhala atafa pofika mmawa! Ngati Baalayo ndi mulungudi, musiyeni adzimenyere yekha nkhondo popeza munthu wina wamugwetsera guwa lansembe lake.” Choncho tsiku limenelo Gideoni anatchedwa, Yeru-Baala, kutanthauza kuti, “Baala alimbana naye, popeza anagwetsa guwa lake la nsembe.” Tsopano Amidiyani, Amaleki ndi anthu ena akummawa anasonkhana ndipo atawoloka Yorodani anakamanga zinthando za nkhondo ku chigwa cha Yezireeli. Ndipo Mzimu wa Yehova unatsikira pa Gideoni, ndipo anayimba lipenga kuyitana Abiezeri kuti amutsatire iye. Iye anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Manase kuti akamenye nkhondo ndipo Amanase anayitanidwanso kuti amutsate. Anatumanso amithenga kwa Aseri, Azebuloni ndi Anafutali, ndipo onsewo anapita kukakumana naye. Gideoni anati kwa Mulungu, “Ngati mudzapulumutsa Israeli ndi dzanja langa monga mwalonjezeramu, onani, ine ndiyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Ngati mame adzagwera pa ubweya wankhosa pokhapa, pa nthaka ponse pakhala powuma, ndiye ndidziwa kuti mudzapulumutsadi Israeli ndi dzanja langa monga mwanenera.” Ndipo zimenezi zinachitikadi. Gideoni atadzuka mʼmamawa ndi kuwufinya ubweya uja, anafinya madzi odzaza mtsuko. Kenaka Gideoni anati kwa Mulungu, “Musandikwiyire. Mundilole ndiyankhule kamodzi kokhaka. Ndiyeseko kamodzi kokha ndi ubweyawu kuti pa ubweya pokhapa pakhale powuma koma pa nthaka ponse pakhale ponyowa ndi mame.” Ndipo Mulungu anachita zomwezo usiku umenewo. Pa ubweya pokha panali powuma, koma pa nthaka ponse panagwa mame. Gideoni Agonjetsa Amidiyani Yeru-Baala (Gideoni) ndi anthu ake onse anadzuka mʼmamawa nakamanga misasa pambali pa kasupe ku Harodi. Misasa ya Amidiyani inali mʼchigwa kumpoto kwa phiri la More. Yehova anati kwa Gideoni, “Anthu uli nawowa andichulukira kwambiri kuti ndigonjetse Amidiyani chifukwa Aisraeli angamadzitukumule pamaso panga ndi kumanena kuti, ‘Tadzipulumutsa ndi mphamvu zathu.’ Tsono lengeza kwa anthu kuti, ‘Aliyense amene akuchita mantha ndi kunjenjemera abwerere kwawo, ndipo achoke kuno ku phiri la Giliyadi.’ ” Choncho anthu 22,000 anachoka, ndipo anatsalira anthu 10,000. Koma Yehova anawuza Gideoni kuti, “Anthuwa achulukabe. Uwatenge upite nawo ku mtsinje ndipo ndikawayesa kumeneko mʼmalo mwako. Ndikadzanena kuti, ‘Uyu apite nawe’ adzapita nawe; koma ndikanena kuti ‘Uyu asapite nawe,’ sadzapita nawe.” Choncho Gideoni anatenga anthuwo ndi kupita nawo ku madzi. Kumeneko Yehova anamuwuza kuti, “Amene amwe madzi mokhathira ndi manja ngati galu uwayike pawokha, ndipo amene amwe atagwada pansi uwayikenso pawokha.” Ndipo anthu 300 anamwa mokhathira, pamene ena onse anagwada pansi pakumwa. Yehova anati kwa Gideoni, “Ndi anthu 300 amene anamwa madzi mokhathira ndi manja awo ndidzakupulumutsani ndipo ndidzapereka Amidiyani mʼmanja mwanu. Koma anthu ena onse apite ku nyumba kwawo.” Choncho analola anthu ena onse kuti apite ku nyumba zawo kupatula anthu 300 osankhika aja. Iwowa anatenga zakudya ndi malipenga a anthuwo. Ndipo misasa ya ankhondo Amidiyani inali kumunsi kwa chigwa. Usiku umenewo Yehova anati kwa Gideoni, “Dzuka, pita kachite nkhondo ku misasayo, chifukwa ndayipereka mʼmanja mwako. Ngati ukuopa, upite ku msasako ndi Pura wantchito wako, ndipo ukamvere zimene akunena ndipo pambuyo pake udzalimba mtima ndi kupita kukayithira nkhondo misasayo.” Choncho iye ndi wantchito wake Pura anapita kumbali ina ya msasawo kumene kunali ankhondo. Amidiyani, Aamaleki ndi anthu ena onse akummawa anadzaza chigwa chonse ngati dzombe. Ngamira zawo zinali zambiri zosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Gideoni atafika anangomva munthu wina akuwuza mnzake maloto ake kuti, “Ine ndinalota nditaona dengu la buledi wa barele likugubuduzika kupita ku misasa ya Amidiyani. Litafika linawomba tenti moti inagwa ndi kuphwasukaphwasuka.” Ndipo mnzakeyo anamuyankha kuti, “Iyi ndi nkhondo ya Gideoni mwana wa Yowasi, wa ku Israeli. Mulungu wapereka Amidiyani pamodzi ndi ankhondo ake onse mʼdzanja mwake.” Gideoni atamva za malotowo ndi kumasulira kwake, anapembedza Mulungu. Kenaka anabwerera ku msasa wa Israeli nawawuza kuti, “Dzukani popeza Yehova wapereka msasa wa Midiyani mʼmanja mwanu.” Anawagawa anthu 300 aja magulu atatu, nawapatsa malipenga mʼmanja mwawo ndi mbiya zimene mʼkati mwake munali nsakali zoyaka. Anawuza anthuwo kuti, “Muzikayangʼana ine ndi kuchita zimene ndizikachita. Ndikakafika kumalire a msasa, mukachite zomwe ndikachita ine. Ndikadzaliza lipenga ndi onse amene ali ndi ine, inunso mukalize malipenga kumbali zonse za misasa yonse ndi kufuwula kuti, ‘Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.’ ” Choncho Gideoni pamodzi ndi amuna 100 omwe anali nawo anafika ku malire a msasa pakati pa usiku, alonda atangosinthana kumene. Iwo analiza malipenga awo ndi kuphwanya mbiya zimene zinali mʼmanja mwawo. Magulu awiri ena aja anayimbanso malipenga ndi kuswa mbiya zawo. Aliyense ananyamula nsakali ya moto ku dzanja lamanzere ndi lipenga ku dzanja lamanja ndipo anafuwula kuti, “Lupanga la Yehova ndi la Gideoni.” Aliyense anayima pa malo pake kuzungulira misasa. Ankhondo a mʼmisasa muja anadzuka nayamba kuthawa akufuwula. Anthu 300 aja ataliza malipenga, Yehova anawasokoneza ankhondo a Midiyani aja motero kuti ankamenyana okhaokha. Ankhondowo anathawira ku Beti-Sita cha ku Zerera mpaka ku malire a Abeli-Mehola pafupi ndi Tabati. Aisraeli a fuko la Nafutali, fuko la Aseri, ndi fuko lonse la Manase anayitanidwa, ndipo iwo anathamangitsa Amidiyaniwo. Gideoni anatumiza amithenga ku dziko lonse la ku mapiri la Efereimu kukanena kuti, “Tsikani mumenyane ndi Amidiyani ndipo mulande madooko awo owolokera mpaka ku Beti-Bara.” Choncho anthu onse a fuko la Efereimu anasonkhana ndipo analanda madooko awo owolokera mpaka ku Betibaala. Iwo anagwiranso atsogoleri awiri a nkhondo a Amidiyani, Orebu ndi Zeebu. Anapha Orebu ku thanthwe la Orebu, koma Zeebu anamuphera ku malo ofinyira mphesa ku Zeebu pothamangitsa Amidiyani. Mitu ya Orebu ndi Zeebu anabwera nayo kwa Gideoni kutsidya kwa Yorodani. Zeba ndi Zalimuna Aefereimu anafunsa Gideoni kuti, “Nʼchifukwa chiyani watichita zimenezi? Bwanji sunatiyitane pamene umakamenyana ndi Amidiyani?” Iwo anamudzudzula kwambiri. Koma iye anawayankha kuti, “Nʼchiyani ndachita kuyerekeza ndi zimene mwachita inu? Kodi zimene mwachita inu Aefereimu si zazikulu kuposa zimene fuko langa la Abiezeri lachita? Mulungu wapereka mafumu a Midiyani, Orebu ndi Zeebu mʼmanja mwanu. Ndachita chiyani kuyerekeza ndi zimene mwachita inu?” Atanena izi, anthuwo mitima yawo inatsika. Gideoni anafika ndi kuwoloka mtsinje wa Yorodani pamodzi ndi anthu 300 amene anali naye. Ngakhale kuti anali otopa anapirikitsabe adani awo. Atafika ku Sukoti anapempha anthu a kumeneko kuti, “Chonde apatseniko buledi ankhondo angawa pakuti atopa. Koma ine ndikupirikitsa Zeba ndi Zalimuna, mafumu a Midiyani.” Koma atsogoleri a Sukoti anayankha kuti, “Kodi Zeba ndi Zalimuna mwawagonjetsa kale kuti tipatse buledi ankhondo akowa?” Gideoni anayankha kuti, “Mwatero! Yehova akapereka Zeba ndi Zalimuna mʼdzanja langa, ndidzakukwapulani ndi matsatsa a minga ya mʼchipululu.” Atachoka pamenepo anapita ku Penueli ndipo anapemphanso buledi kwa anthu a kumeneko, koma iwo anamuyankha monga anayankhira anthu a ku Sukoti aja. Gideoni anawawuzanso kuti, “Ndikamadzabwerera nditawagonjetsa, ndidzagwetsa nsanja iyi.” Nthawi iyi nʼkuti Zeba ndi Zalimuna ali ku Karikori ndi ankhondo pafupifupi 15,000. Amenewa ndiwo anatsalako mwa ankhondo a anthu akummawa; pakuti anafa ankhondo 120,000. Gideoni anadzera njira ya anthu a matenti kummawa kwa Noba ndi Yogibeha ndipo anawathira nkhondo popeza ankhondo awo anali osakonzekera. Zeba ndi Zalimuna, mafumu awiri a Amidiyani anathawa koma Gideoni anawathamangitsa mpaka kuwagwira. Koma ankhondo awo onse anathawa ndi mantha. Ndipo Gideoni mwana wa Yowasi, pobwera kuchokera ku nkhondo anadzera njira ya ku chikweza cha Heresi. Kumeneko iye anagwira mnyamata wa ku Sukoti ndipo atamufunsa, mnyamatayo anamulembera mayina a akuluakulu ndi atsogoleri 77 a ku Sukoti. Kenaka Gideoni anabwera kwa anthu a ku Sukoti ndi kunena kuti, “Awa ndi Zeba ndi Zalimuna, mafumu awiri munkandinena nawo aja kuti, ‘Kodi Zeba ndi Zalimuna wawagonjetsa kale mmene ukuti tiwapatse buledi anthu ako otopawa?’ ” Tsono Gideoni anatenga akuluakulu a mu mzindawo ndipo anagwira matsatsa a minga za mʼchipululu ndi kuwakwapula nawo. Anagwetsa nsanja ya ku Penueli ndi kupha amuna onse a mu mzindawo. Kenaka anafunsa Zeba ndi Zalimuna kuti, “Kodi anthu a ku Tabori amene munawapha aja anali a maonekedwe otani?” Iwo anayankha kuti, “Anali anthu a maonekedwe ngati inu. Aliyense ankaoneka ngati mwana wa mfumu?” Iwo anayankha kuti, “Anthu ngati inu, aliyense wooneka ngati mwana wa mfumu.” Ndipo Gideoni anayankha kuti, “Ndikulumbira pa Mulungu, mukanapanda kuwapha nanenso sindikanakuphani. Ndi abale anga amenewo, ana a amayi anga enieni.” Tsono anawuza Yetero, mwana wake wachisamba kuti, “Tiye, ipha anthu amenewa!” Koma chifukwa Yeteri anali wamngʼono sanasolole lupanga lake, popeza anachita mantha. Tsono Zeba ndi Zalimuna anawuza Gideoni kuti, “Bwera utiphe ndiwe chifukwa uli ndi mphamvu za munthu wamkulu.” Choncho Gideoni anapita nawapha natenganso zokongoletsera zimene zinali pa makosi a ngamira zawo. Efodi ya Gideoni Aisraeli anati kwa Gideoni, “Inu muzitilamulira, mwana wanu ndi zidzukulu zanu, chifukwa mwatipulumutsa mʼmanja mwa Amidiyani.” Koma Gideoni anawawuza kuti, “Sindidzakulamulirani, mwana wanganso sadzakulamulirani. Koma Yehova ndiye adzakulamulirani.” Gideoni anatinso, “Ine ndikupemphani chinthu chimodzi. Aliyense wa inu andipatse ndolo zomwe anafunkha ku nkhondo.” (Adani aja anali ndi ndolo zagolide popeza anali Aismaeli). Iwo anayankha kuti, “Ife tikupatsani ndithu ndolozi.” Choncho anayala chinsalu, ndipo aliyense anaponyapo ndolo zimene anafunkha. Tsono kulemera kwa ndolo zagolide zimene anapereka kunali makilogalamu makumi awiri, osawerengera kulemera kwa mphande, mkanda wamʼkhosi, zovala zapepo za mafumu a Midiyani ndiponso malamba azitsulo za mʼmakosi a ngamira zawo. Gideoni anagwiritsa ntchito golide uja kupanga efodi, ndipo anakamuyika ku mzinda wake ku Ofura. Tsono Aisraeli onse anasiya kupembedza Yehova nayamba kupembedza efodiyo kumeneko. Ichi chinasanduka msampha kwa Gideoni ndi banja lake lonse. Imfa ya Gideoni Choncho Amidiyani anagonjetsedwa ndi Aisraeli ndipo sanayeserenso kuwawukira. Ndipo dzikolo linakhala pa mtendere kwa zaka 40 pamene Gideoni anali ndi moyo. Yeru-Baala mwana wa Yowasi anapita kukakhala kwawo. Ana a Gideoni anali 70 popeza anali ndi akazi ambiri. Mdzakazi wake amene anali ku Sekemu, anabereka naye mwana wamwamuna, amene anamutcha Abimeleki. Gideoni mwana wa Yowasi anamwalira atakalamba ndipo anayikidwa mʼmanda a abambo ake, Yowasi ku Ofura mzinda wa Mwabiezeri. Atangomwalira Gideoni, Aisraeli anayambanso kupembedza Abaala. Iwo anasandutsa Baala-Beriti kukhala mulungu wawo. Aisraeli sanakumbukirenso Yehova Mulungu wawo amene anawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo mbali zonse. Ndiponso sanachite zinthu zokomera banja la Yeru-Baala (ndiye kuti Gideoni) chifukwa cha zabwino zonse zimene iye anawachitira. Abimeleki Abimeleki mwana wa Yeru-Baala anapita ku Sekemu kwa abale a amayi ake ndi kukawawuza iwowo ndi fuko lonse la banja la abambo a amayi ake kuti, “Funsani nzika zonse za ku Sekemu kuno, ‘Chabwino ndi chiyani kwa inu kuti ana onse makumi asanu ndi awiri a Yeru-Baala azikulamulirani, kapena kuti azikulamulirani ndi munthu mmodzi basi?’ Kumbukirani kuti ine ndine mʼbale wanu weniweni.” Abale a amayi akewo anamuyankhulira mawu amenewa kwa nzika zonse za ku Sekemu, ndipo mitima ya anthu onse inali pa Abimeleki chifukwa anati, “Uyu ndi mʼbale wathu,” Tsono anamupatsa ndalama zasiliva 70 za mʼnyumba ya chipembedzo ya Baala Beriti. Ndi ndalama zimenezi Abimeleki analemba anthu achabechabe ndi osasamala kuti azimutsatira. Anapita ku Ofiri ku mudzi kwa abambo ake ndipo anapha abale ake makumi asanu ndi awiri, ana a Yeru-Baala pa mwala umodzi. Koma Yotamu yemwe anali wamngʼono mwa onsewo anapulumuka chifukwa anabisala. Tsono nzika za ku Sekemu ndi za ku Beti-Milo zinapita kukasonkhana ku mtengo wa thundu pafupi ndi chipilala cha ku Sekemu kuti akalonge Abimeleki ufumu. Yotamu atamva izi anapita kukayima pamwamba pa phiri la Gerizimu ndipo anafuwula nati, “Tandimverani inu anthu a ku Sekemu, kuti Mulungu akumvereninso. Tsiku lina mitengo inapita kukadzoza mfumu yawo. Tsono mitengoyo inati kwa mtengo wa olivi, ‘Iwe ukhale mfumu yathu.’ ” “Koma mtengo wa olivi uja unayankha kuti, ‘Kodi ndisiye mafuta angawa amene amalemekezera nawo milungu ndi anthu omwe, kuti ndizikalamulira mitengo?’ ” Apo mitengo inawuza mtengo wa mkuyu kuti, “Bwera ndiwe ukhale mfumu yathu.” Koma mtengo wa mkuyu unayankha kuti, “Kodi ndisiye chipatso changa chokoma ndi chozunachi kuti ndizikalamulira mitengo?” Kenaka mitengo ija inawuza mtengo wamphesa kuti, “Bwera ndiwe kuti ukhale mfumu yathu.” Koma mtengo wamphesa unayankha kuti, “Kodi ine ndisiye vinyo wangayu, amene amasangalatsa milungu ndi anthu omwe kuti ndizikalamulira mitengo?” Pomaliza mitengo yonse inawuza mkandankhuku kuti, “Bwera ndipo ukhale mfumu yathu.” Mkandankhuku uja unayankha kuti, “Ngati mukufunadi kuti mudzoze ine kuti ndikhale mfumu yanu, bwerani mudzabisale mu mthunzi mwangamu, koma ngati simutero, moto utuluka kwa ine ndi kupsereza mikungudza ya ku Lebanoni.” Yotamu anatinso, “Kodi mukuti munaonetsadi kuona mtima ndi kukhulupirika podzoza Abimeleki kukhala mfumu? Kodi mukuti munachitira ulemu Yeru-Baala ndi banja lake poganizira ntchito zimene anachita? Kodi suja abambo anga anakumenyerani nkhondo ndi kuyika moyo wawo pa chiswe kuti akupulumutseni mʼmanja mwa Amidiyani? Koma lero inu mwawukira banja la abambo anga. Mwapha ana ake 70 pa mwala umodzi, ndiponso mwalonga ufumu Abimeleki, mwana wa mdzakazi wake kuti akhale wolamulira anthu a ku Sekemu chifukwa ndi mʼbale wanu. Tsono ngati mukuti zimene mwachitira Yeru-Baala ndi banja lake mwazichita moona mtima ndiponso mokhulupirika, ndiye mukondwere ndi Abimeleki, nayenso akondwere nanu! Koma ngati sichoncho moto utuluke mwa Abimeleki ndi kupsereza anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndipo moto utulukenso mwa anthu a ku Sekemu ndi Beti-Milo, ndi kupsereza Abimeleki!” Kenaka Yotamu anathawira ku Beeri nakakhala komweko chifukwa ankaopa Abimeleki mʼbale wake. Abimeleki atalamulira Israeli zaka zitatu, Mulungu anayika chidani pakati pa Abimelekiyo ndi anthu a ku Sekemu, motero kuti anthu a ku Sekemu anawukira Abimeleki. Mulungu anachita zimenezi kuti zoyipa zimene anachitira ana aamuna 70 a Yeru-Baala aja zimubwerere, ndi kuti magazi awo akhale pa Abimeleki mʼbale wawo ndi pa anthu a ku Sekemu amene anamulimbikitsa mtima kuti aphe abale akewo. Choncho anthu a ku Sekemu anayika anthu omubisalira pamwamba pa mapiri. Tsono iwo ankalanda anthu odutsa mʼnjira imeneyo zinthu zawo ndipo Abimeleki anamva zimenezi. Gaali mwana wa Ebedi anasamukira ku Sekemu ndi abale ake, ndipo anthu a ku Sekemuko anamukhulupirira iye. Anthuwo anapita ku munda kukathyola mphesa ndi kuzifinya, ndipo anachita chikondwerero mʼnyumba ya milungu yawo. Anthuwo akudya ndi kumwa, ankatemberera Abimeleki. Ndipo Gaali mwana wa Ebedi anati “Kodi Abimeleki ndi ndani, ndipo nʼchifukwa chiyani akutilamulira ife Asekemu? Kodi iyeyu si mwana wa Yeru-Baala ndipo womuthandiza wake si Zebuli? Tiyeni titumikire anthu a ku Hamori, kholo la fuko la Sekemu! Nanga nʼchifukwa chiyani tikutumikira Abimeleki? Anthu a mu mzindawo akanakhala pansi pa ulamuliro wanga, ndikanamuchotsa Abimelekiyu. Ndikanamuwuza Abimeleki kuti, ‘Wonjeza ankhondo ako ndipo ubwere tidzamenyane!’ ” Zebuli amene ankalamulira mzindawo atamva zimene Gaali mwana wa Ebadi ananena, anakwiya kwambiri. Anatumiza amithenga kwa Abimeleki, kukanena kuti, “Gaali mwana wa Ebedi ndi abale ake abwera ku Sekemu ndipo akuwutsa mitima ya anthu a mu mzindawo kuti akuwukireni inu. Nʼchifukwa chake usiku womwe uno inu ndi anthu anu mupite, mukabisale mʼminda. Mmawa dzuwa likutuluka, mudzuke ndi kukathira nkhondo mzindawo. Gaali ndi anthu amene ali naye akamadzabwera kuti alimbane ndi inu, inu mudzathane nawo monga mmene mungachitire.” Choncho Abimeleki ndi ankhondo ake onse anadzuka usiku nakabisalira mzinda wa Sekemu mʼmagulu anayi. Gaali mwana wa Ebedi anatuluka nakayima pa khomo pa chipata cha mzinda pamene Abimeleki ndi ankhondo ake anatuluka ku malo kumene anabisala kuja. Gaaliyo atawaona, anawuza Zebuli kuti, “Taona anthu akutsika kuchoka pamwamba pa mapiri.” Koma Zebuli anayankha kuti, “Zimene mukuonazo ndi zithunzi za mapiri chabe osati anthu.” Koma Gaaliyo anayankhulanso kuti, “Taona anthu akutsika kuchokera pakati pa phiri, ndipo gulu lina likubwera kuchokera ku mtengo wa thundu wa owombeza mawula.” Ndipo Zebuli anamufunsa iye kuti, “Pakamwa pako paja pali kuti tsopano, iwe amene umanena kuti, Abimeleki ndaninso kuti ife timutumikire? Kodi amenewa si anthu aja umawanyozawa? Tsopano tuluka ukamenyane nawo.” Choncho Gaaliyo anatuluka akutsogolera anthu a ku Sekemu kukamenyana ndi Abimeleki. Koma Abimeleki anamuthamangitsa ndipo Gaala anathawa. Ambiri a ankhondo ake anagwa napwetekeka njira yonse mpaka ku chipata cha mzinda. Abimeleki anakhala ku Aruma, ndipo Zebuli anathamangitsa Gaali pamodzi ndi abale ake, kuwatulutsa mu Sekemu. Mmawa mwake anthu a ku Sekemu anapangana zopita ku minda, ndipo Abimeleki anamva zimenezi. Tsono Abimeleki anatenga anthu ake, nawagawa magulu atatu ndi kukabisala mʼminda. Ataona anthu akutuluka mu mzindawo, iye anapita kukalimbana nawo ndipo onsewo anawapha. Abimeleki pamodzi ndi magulu ake anathamangira kutsogolo nakawakhalira pa chipata cha mzinda. Ndipo magulu awiri ena aja anathamangira anthu amene anali mʼminda ndi kuwapha onse. Abimeleki anawuthira nkhondo mzindawo tsiku lonse. Kenaka anawulanda ndi kupha nzika zonse za mu mzindamo. Anawuwonongeratu mzindawo nawuwaza mchere. Anthu a mu nsanja ya Sekemu atamva zimenezi, anakalowa mu linga la nyumba yopembedzeramo Baala-Beriti. Abimeleki anamva kuti anthu ena asonkhana kumeneko. Choncho Abimeleki pamodzi ndi anthu ake onse anapita ku phiri la Zalimoni. Kumeneko anatenga nkhwangwa nadula nthambi za mitengo. Ananyamula nthambi zija pa phewa pake. Tsono anawuza anthu aja kuti, “Zimene mwaona ine ndikuchita, inunso mufulumire kuchita monga ndachitiramu.” Tsono aliyense anadula nthambi zake, natsatira Abimeleki. Anakawunjika nthambi zija pa linga paja, kenaka ndi kuliyatsa moto. Choncho anthu onse a ku nsanja ya Sekemu anafa. Analipo anthu pafupifupi 1,000, amuna ndi akazi. Kenaka Abimeleki anapita ku Tebezi. Anakawuzungulira mzindawo ndi kuwulanda. Koma mu mzindamo munali nsanja yolimba. Anthu onse a mu mzindamo amuna ndi akazi anathawira mu nsanjayo, nadzitsekera mʼkati. Ndipo anakwera ku denga la nsanjayo. Abimeleki anapita ku nsanjayo nathira nkhondo. Anafika pafupi ndi chitseko cha nsanja ija kuti ayitenthe. Koma mkazi wina anaponya mwala wa mphero pa mutu wa Abimeleki ndi kuswa chibade cha mutuwo. Mwamsanga Abimeleki anayitana mnyamata womunyamulira zida za nkhondo namuwuza kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuti anthu asadzanene kuti, ‘Mkazi ndiye anamupha.’ ” Choncho wantchito wake anamubayadi mpaka kutulukira kunja lupangalo ndipo anafa. Aisraeli ataona kuti Abimeleki wafa, anapita kwawo. Mmenemu ndi mmene Mulungu analipsirira tchimo la Abimeleki limene anachitira abambo ake pakupha abale ake 70 aja. Mulungu anawalanganso anthu a ku Sekemu chifukwa cha kuyipa kwawo konse. Ndipo matemberero a Yotamu mwana wa Yeru-Baala anawagweradi. Tola Atafa Abimeleki panabwera Tola mwana wa Puwa, mdzukulu wa Dodo kudzapulumutsa Aisraeli. Iyeyu anali wa fuko la Isakara ndipo ankakhala ku Samiri mʼdziko la mapiri la Efereimu. Iye anatsogolera Aisraeli kwa zaka 23, ndipo anamwalira ndi kuyikidwa ku Samiri. Yairo Atafa Tola panabwera Yairi wa ku Giliyadi, amene anatsogolera Israeli kwa zaka 22. Iyeyu anali ndi ana aamuna makumi atatu, amene ankakwera pa abulu makumi atatu. Iwo anali ndi mizinda makumi atatu mʼdziko la Giliyadi, imene mpaka lero ikutchedwa kuti Havoti Yairi. Atamwalira Yairi anayikidwa mʼmanda ku Kamoni. Yefita Aisraeli anachitanso zoyipira Yehova. Iwo anatumikira Abaala ndi Asitoreti, milungu ya ku Aramu, Sidoni, Mowabu, Aamoni ndi Afilisti. Choncho analeka osatumikiranso Yehova. Tsono Yehova anapsera mtima Aisraeli ndipo anawapereka mʼmanja mwa Afilisti ndi Aamoni. Iwowa anawagonjetseratu Aisraeli mʼchaka chimenechi, ndipo kwa zaka 18 anakhala akusautsa Aisraeli onse amene anali pa tsidya la Yorodani, mʼdziko la Aamori ku Giliyadi. Aamori anawoloka mtsinje wa Yorodani kukathira nkhondo mafuko a Yuda, Benjamini ndi Efereimu kotero kuti Israeli anavutika kwambiri. Kenaka Aisraeli analira kwa Yehova kuti, “Ife takuchimwirani popeza tasiya Inu Mulungu wathu ndi kutumikira Abaala.” Yehova anawafunsa kuti, “Suja ine ndinakupulumutsani kwa Aigupto, Aamori, Aamoni ndi Afilisti? Ndiponso pamene Asidoni, Aamaleki ndi Amoni anakuzunzani, inu nʼkulirira kwa ine suja ndinakupulumutsani kwa anthu amenewa? Komabe inu mwandikana ndipo mukutumikira milungu ina. Choncho sindidzakupulumutsaninso. Pitani kalireni kwa milungu imene mwayisankha. Iyoyo ikupulumutseni ku mavuto anuwo.” Koma Aisraeli anayankha Yehova kuti, “Ife tachimwa. Tichitireni chimene mukuona kuti ndi chabwino, koma chonde tipulumutseni lero lokha.” Ndipo anachotsa milungu ya chilendo pakati pawo ndi kuyamba kutumikira Yehova. Ndipo Yehova anamva chisoni poona mmene Aisraeli ankazunzikira. Tsono Aamoni anasonkhana ndi kumanga zithando za nkhondo ku Giliyadi. Nawonso Aisraeli anasonkhana ndi kumanga zithando zawo za nkhondo ku Mizipa. Kenaka anthuwo ndi atsogoleri a Agiliyadi anayamba kufunsana kuti, “Kodi ndi munthu wotani amene atayambe kuthira nkhondo Aamoni? Iyeyu adzakhala mtsogoleri wolamulira anthu onse a ku Giliyadi.” Yefita wa ku Giliyadi anali wankhondo wa mphamvu. Iyeyu amayi ake anali mkazi wachiwerewere, ndipo abambo ake anali Giliyadi. Mkazi wake wa Giliyadi anabereka naye ana aamuna. Tsono ana amenewa atakula anapirikitsa Yefita ndi kumuwuza kuti, “Sudzalandirako cholowa mʼnyumba ya abambo athu chifukwa ndiwe mwana wa mkazi wina.” Choncho Yefita anathawa kuchoka kwa abale ake ndi kukakhala mʼdziko la Tobu. Kumeneko anakakopa ndi kusonkhanitsa anthu achabechabe ndipo anatuluka pamodzi kukasakaza zinthu. Patapita nthawi Aamoni anadzachita nkhondo ndi Israeli. Tsono pamene Aamoni ankathira nkhondo Aisraeli, akuluakulu a ku Giliyadi anapita kukamutenga Yefita ku dziko la Tobu. Iwo anati kwa iye, “Bwera ukhale mkulu wathu wankhondo kuti timenyane ndi Amoni.” Yefita anawawuza Agiliyadi kuti, “Kodi inu suja munkadana nane ndi kundithamangitsa ku nyumba ya abambo anga? Nʼchifukwa chiyani lero mwabwera kwa ine pamene muli pa mavuto?” Akuluakulu a ku Giliyadi aja anamuyankha kuti, “Chimene tabwerera kwa iwe ndi chakuti upite nafe kukamenyana ndi Aamoni, ndipo udzakhala wolamulira wa onse okhala mu Giliyadi.” Yefita anawayankha akuluakulu a ku Giliyadi kuti, “Ngati mundibwezeranso kwathu kuti ndikachite nkhondo ndi Aamoni ndipo Yehova nʼkukandithandiza kuwagonjetsa, ndidzakhaladi wokulamulirani?” Akuluakulu a ku Giliyadi anamuyankha kuti, “Yehova akhale mboni pakati pa inu ndi ife, ngati sitidzachita monga mwa mawu anu.” Choncho Yefita anapita nawo akuluakulu a ku Giliyadi aja, ndipo anthu a kumeneko anamusandutsa kukhala wowalamulira ndi mkulu wankhondo. Tsono Yefita anabwerezanso mawu omwewa pamaso pa Yehova ku Mizipa. Kenaka Yefita anatuma amithenga kwa mfumu ya Aamoni ndi funso lakuti, “Kodi ife takuchimwirani chiyani kuti muzichita nkhondo ndi dziko langa?” Ndipo mfumu ya Aamoni inayankha amithenga a Yefita aja kuti, “Pamene Israeli amatuluka kuchokera mu Igupto, analanda dziko langa kuyambira ku mtsinje wa Arinoni mpaka ku mtsinje wa Yaboki mpakanso ku mtsinje wa Yorodani. Tsopano mundibwezere dziko langa mwamtendere.” Yefita anatumizanso amithenga akewo kwa mfumu ya Aamoni kukanena kuti, Yefita akuti, “Israeli sanalande dziko la Mowabu kapena dziko la Aamoni. Koma pamene Aisraeli ankachoka ku Igupto anadzera njira ya ku chipululu mpaka ku Nyanja Yofiira nakafika ku Kadesi. Kenaka Israeli anatumiza amithenga kwa mfumu ya ku Edomu kuti, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu,’ Koma mfumu ya ku Edomu sinamvere zimenezo. Aisraeli anatumizanso amithenga kwa mfumu ya ku Mowabu, ndipo iyo inakananso. Choncho Israeli anakhala ku Kadesi. “Pambuyo pake, Aisraeli ananyamuka ulendo kudzera ku chipululu nazungulira dziko la Edomu ndi dziko la Mowabu, ndipo anafika ku mmawa kwa dziko la Mowabu ndi kumanga zinthando zawo ku mbali ina ya mtsinje wa Arinoni. Iwo sanalowe mʼdziko la Mowabu, chifukwa mtsinje wa Arinoni ndiwo unali malire a dziko la Mowabu. “Pambuyo pake Israeli anatumiza amithenga kwa Sihoni mfumu ya Aamori, amene amalamulira ku Hesiboni ndipo anati kwa iye, ‘Chonde tiloleni kuti tidutse mʼdziko lanu popita kwathu.’ Koma Sihoni sanalole Israeli kuti adzere mʼdziko mwake. Mʼmalo mwake Sihoni anasonkhanitsa ankhondo ake onse nakamanga msasa ku Yahazi ndipo anachita nkhondo ndi Israeli. “Koma Yehova Mulungu wa Israeli anamupereka Sihoni pamodzi ndi anthu ake onse mʼmanja mwa Israeli, ndipo anawagonjetsa. Choncho Aisraeli analanda dziko lonse la Aamori amene amakhala mʼdzikolo. Analanda dziko lonse kuchokera ku Arinoni mpaka ku Yaboki ndiponso kuchokera ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yorodani. “Ndiye kuti Yehova Mulungu wa Aisraeli ndiye analanda dziko la Aamori, kuwalandirira anthu ake. Kodi inu mukufuna kutilanda dzikolo? Bwanji inu osakhazikika mʼdziko limene Kemosi mulungu wanu anakupatsani, ifenso tikhazikike mʼdziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa? Kodi ndinu abwino kuposa Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu? Kodi iye anakanganapo kapena kuchita nkhondo ndi Israeli? Pamene Aisraeli ankakhala mʼdziko la Hesiboni ndi mʼmidzi yake, mʼdziko la Aroeri ndi midzi yake, komanso mʼmizinda yonse imene ili mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni kwa zaka 300, nʼchifukwa chiyani inu simunalande malowo nthawi imeneyo? Choncho ine sindinakuchimwireni. Koma inu mukundilakwira pomenyana nane. Yehova woweruza, ndiye aweruze lero mlandu wa pakati pa Aisraeli ndi Aamoni.” Koma mfumu ya Aamori, sinasamale mawu amene Yefita anatumiza kwa iyo. Tsono Mzimu wa Yehova unatsikira pa Yefita. Ndipo iye ananyamuka nadzera ku Giliyadi ndi ku Manase. Anafika ku Mizipa mʼdziko la Giliyadi, ndipo kuchokera kumeneko anapita kukalimbana ndi Aamoni. Yefita analumbira kwa Yehova kuti, “Ngati mupereka Aamoni mʼmanja mwanga, aliyense amene atuluke pa khomo la nyumba yanga kudzandichingamira pobwerera nditagonjetsa Aamoni adzakhala wake wa Yehova, ndipo ndidzamupereka kuti akhale nsembe yopsereza.” Kenaka Yefita anawolokera kwa Aamoni kukamenya nawo nkhondo, ndipo Yehova anawaperekadi mʼmanja mwake. Iye anawononga mizinda makumi awiri kuchokera ku Ariori mpaka pafupi ndi mzinda wa Miniti. Anapitirira mpaka ku Abeli-Keranimu. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamoni. Pambuyo pake Yefita anabwerera ku nyumba yake. Tsono anangoona mwana wake wamkazi akutuluka kudzamuchingamira akuyimba ngʼoma ndi kuvina. Uyu anali mwana yekhayo wa Yefita. Analibenso mwana wina wamwamuna kapena wamkazi. Yefita ataona mwana wake uja, anangʼamba zovala zake ndi kulira, “Kalanga ine! Mwana wanga! Wandivulaza kwambiri ndipo iwe ndi gwero la mavuto anga. Ine ndinalumbira kwa Yehova ndi pakamwa pangapa ndipo sindingathe kubweza malumbiro angawo.” Mwanayo anayankha kuti, “Abambo, ngati munalonjeza kwa Yehova ndi pakamwa panu, chitani zimene munalonjezera pakuti Yehova wakuthandizani kulipsira adani anu Amowabu.” Anatinso kwa abambo ake, “Ndikupempheni chinthu ichi: Mundilole ndikayendeyende ku mapiri miyezi iwiri ndizikalira pamodzi ndi anzanga chifukwa ndikufa ndikanali namwali wosadziwa mwamuna.” Yefita anamuyankha kuti, “Pita.” Ndipo anamulola kuti apite miyezi iwiri. Tsono anapita kumapiri ndi atsikana anzake kukalira chifukwa cha unamwali wake. Miyezi iwiri itatha iye anabwerera kwa abambo ake, ndipo anachitadi zimene analonjeza. Motero unakhala mwambo wa Aisraeli, kuti atsikana a Israeli ankapita chaka chilichonse kukalira maliro a mwana wa mkazi wa Yefita, Mgiliyadi uja masiku makumi anayi pa chaka. Yefita ndi Aefereimu Gulu la nkhondo la fuko la Efereimu linayitanidwa ndipo anawolokera ku Zafoni nakafunsa Yefita kuti, “Nʼchifukwa chiyani unawoloka kukachita nkhondo ndi Aamoni osatiyitana kuti tipite nawe? Ife tikutenthera mʼnyumba mwakomu.” Yefita anayankha kuti, “Ine ndi anthu anga tinakangana kwambiri ndi Aamoni. Ndinakuyitanani koma inu simunandipulumutse mʼmanja mwawo. Nditaona kuti simundithandiza, ndinayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndinawoloka kukachita nkhondo ndi a Aamoni. Yehova anandithandiza ndipo ndinawagonjetsa. Nanga nʼchifukwa chiyani mwabwera kwa ine lero kuti muchite nane nkhondo?” Choncho Yefita anasonkhanitsa anthu a ku Giliyadi ndi kuchita nkhondo ndi Aefereimu. Ndipo Agiliyadi anagonjetsa Aefereimu chifukwa Aefereimuwo amati, “Inu a Giliyadi ndinu othawa kuchokera ku Efereimu ndi pakati pa Amanase.” Choncho Agiliyadi analanda Aefereimu madooko a mtsinje wa Yorodani. Munthu aliyense wothawa ku Efereimu amati akanena kuti, “Ndiloleni ndiwoloke,” Agaliyadi ankafunsa kuti, “Kodi ndiwe mu Efurati?” Ngati iye ayankha kuti, “Ayi” Ndiye amamuwuza kuti, “Nena kuti ‘Shiboleti.’ ” Tsono munthuyo akanena kuti Siboleti popeza samatha kutchula bwino mawuwa, ankamugwira ndi kumupha pomwepo pa madooko a mtsinje wa Yorodani. Nthawi imeneyo anaphedwa Aefereimu 42,000. Yefita anatsogolera Israeli zaka zisanu ndi chimodzi. Kenaka Yefita wa ku Giliyadi anamwalira, ndipo anayikidwa mu mzinda wake ku Giliyadi. Ibizani, Eloni ndi Abidoni Atamwalira Yefita, Ibizani wa ku Betelehemu anatsogolera Israeli. Iye anali ndi ana aamuna makumi atatu ndi ana aakazi makumi atatu. Anakwatitsa ana ake akaziwo kwa anthu a fuko lina, ndipo ana ake aamuna aja anawabweretsera atsikana makumi atatu kuti awakwatire amenenso anali a fuko lina. Ibizani anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Kenaka Ibizani anamwalira, ndipo anayikidwa mu Betelehemu. Iye atamwalira, Eloni wa fuko la Zebuloni anakhala mtsogoleri wa Aisraeli, ndipo anatsogolera Aisraeli kwa zaka khumi. Kenaka Eloni anamwalira ndipo anayikidwa ku Ayaloni mʼdziko la Zebuloni. Iye atamwalira, Abidoni mwana wa Hilelo wochokera ku Piratoni, anatsogolera Israeli. Iye anali ndi ana aamuna makumi anayi ndi zidzukulu makumi atatu, amene ankakwera pa abulu 70. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka zisanu ndi zitatu. Ndipo Abidoni mwana wa Hilelo Mpiratoni uja anamwalira, nayikidwa ku Piratoni, mʼdziko la Efereimu, dziko lamapiri la Aamaleki. Kubadwa kwa Samsoni Aisraeli anachitanso zinthu zoyipira Yehova, kotero Yehova anawapereka mʼmanja mwa Afilisti kwa zaka makumi anayi. Ku Zora kunali munthu wina dzina lake Manowa, wochokera ku fuko la Dani. Mkazi wake analibe ana popeza anali wosabereka. Mngelo wa Yehova anaonekera mkaziyo ndipo anati, “Ndinu wosabereka ndipo mulibedi mwana, komabe mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Tsono mudzisamale bwino, osamwa vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa ndiponso musamadye chakudya chilichonse chodetsedwa, chifukwa mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo akadzabadwa lumo lisadzapite pa mutu chifukwa mnyamatayo adzakhala Mnaziri, ndiye kuti wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero. Ndipo adzayamba ntchito yopulumutsa Israeli mʼmanja mwa Afilisti.” Kenaka mayiyo anapita kukawuza mwamuna wake kuti, “Munthu wa Mulungu anabwera kwa ine, ndipo maonekedwe ake anali ngati mngelo wa Mulungu, maonekedwe woopsa kwambiri. Ine sindinamufunse kumene amachokera, ndipo iyeyo sanandiwuzenso dzina lake. Koma anandiwuza kuti, ‘Mudzakhala ndi pakati ndipo mudzabereka mwana wamwamuna. Choncho musamamwe vinyo kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa, musamadye chakudya chilichonse choyipitsidwa chifukwa mwanayo adzakhala Mnaziri, wopatulika kwa Mulungu kuyambira pa nthawi imene adzakhale ali mʼchiberekero mpaka tsiku la kufa kwake.’ ” Kenaka Manowa anapemphera kwa Yehova kuti, “Chonde Ambuye, lolani munthu wa Mulungu amene munamutuma abwerenso kwa ife kuti adzatiphunzitse zochita ndi mwanayo akadzabadwa.” Mulungu anamva pemphero la Manowa, ndipo mngelo wa Mulungu anabweranso kwa mkaziyo nthawi imene anali ku munda, koma Manowa mwamuna wake sanali naye. Tsono mkaziyo anathamanga kukawuza mwamuna wake kuti, “Wandionekeranso munthu uja amene anabwera kwa ine tsiku lija.” Choncho Manowa ananyamuka namutsatira mkazi wake. Atafika kwa munthuyo anamufunsa kuti, “Kodi ndinu munayankhula ndi mkazi wanga?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Kenaka Manowa anafunsa kuti, “Tiyerekeze kuti mawu anuwa akwaniritsidwadi, ndiye mwanayu azidzakhala bwanji ndipo azidzachita chiyani?” Ndipo mngelo wa Yehova uja anamuyankha kuti, “Zonse zimene ndinawawuza akazi anuwa asamale ndipo adzazichitedi. Asadzadye chilichonse chochokera ku mphesa. Asadzamwe vinyo kapena choledzeretsa chilichonse, ngakhale kudya chakudya chilichonse chodetsedwa. Zonse zimene ndinawalamula azisunge bwino.” Manowa anamuwuza mngelo wa Yehova uja kuti, “Chonde dikirani pangʼono, timati tikukonzereni mwana wambuzi.” Mngelo wa Yehova anayankha kuti, “Ngakhale mukundidikiritsa, ine sindidya chakudya chanu. Koma ngati mukonze nsembe yopsereza iperekeni kwa Yehova.” (Manowa nʼkuti asakudziwa kuti munthuyo anali mngelo wa Mulungu). Tsono Manowa anapempha mngelo wa Yehova kuti, “Chonde tidziwitseni dzina lanu kuti zikadzachitika zimene mwanenazi ife tidzakulemekezeni?” Iye anayankha kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukufunsa dzina langa? Dzina laketu ndi lodabwitsa.” Ndipo Manowa anatenga mwana wambuzi pamodzi ndi chopereka cha chakudya nakapereka nsembe pa thanthwe kwa Yehova ndipo Yehova anachita zodabwitsa kwa Manowa ndi mkazi wake akuona. Pamene malawi a moto amakwera kumwamba kuchoka pa guwa, mngelo wa Yehova uja anakwera kumwamba mʼmalawi a motowo Manowa ndi mkazi wake akuona. Tsono anadzigwetsa pansi naweramitsa mitu yawo pansi. Mngelo wa Yehova uja sanaonekerenso kwa Manowa ndi mkazi wake. Choncho Manowa anazindikira kuti anali mngelo wa Yehova. Iye anawuza mkazi wake kuti, “Ife tifa basi pakuti taona Mulungu!” Koma mkazi wake anamuyankha kuti, “Yehova akanafuna kutipha sakanayilandira nsembe yathu yopsereza ndi chopereka chathu chachakudya chija, ndipo sakanationetsanso zinthu zonsezi kapena kutiwuza zinthu ngati zimenezi nthawi ino.” Motero mkaziyo anabereka mwana wa mwamuna, namutcha dzina lake Samsoni. Iye anakula ndipo Yehova anamudalitsa. Mzimu wa Yehova unayamba kumulimbikitsa pamene ankakhala ku misasa ya anthu a fuko la Dani, malo amene anali pakati pa Zora ndi Esitaoli. Ukwati wa Samsoni Samsoni anapita ku Timna ndipo kumeneko anaonako mtsikana wa Chifilisiti. Atabwerera kwawo, anawuza abambo ndi amayi ake kuti, “Ine ndaona mtsikana wa Chifilisiti ku Timna, tsono mukanditengere ameneyo kuti akhale mkazi wanga.” Koma abambo ndi amayi ake anayankha kuti, “Kodi palibe mkazi pakati pa abale akowa kapena pakati pa anthu a mtundu wako, kuti iwe upite kukapeza mkazi kwa Afilisti anthu osachita mdulidwe?” Koma Samsoni anawuza abambo ake kuti, “Kanditengereni ameneyu basi, pakuti ndamukonda.” (Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli). Choncho Samsoni pamodzi ndi abambo ake anapita ku Timna. Akuyandikira minda ya mpesa ya ku Timna, mwadzidzidzi anamva kubuma kwa mkango waungʼono ukubwera kumene kunali iye. Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo. Kenaka Samsoni anapita kukakambirana ndi mkaziyo, ndipo anamukonda mtsikanayo. Patapita nthawi, Samsoni anabwerera kukatenga mtsikana uja. Panjira anapatuka kukaona mkango unawupha uja, ndipo anangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake. Tsono anakomberako uchi uja mʼmanja mwake ndi kumapita akudya. Atabwereranso kwa abambo ndi amayi ake, anawapatsako uchiwo ndipo anadya. Koma sanawawuze kuti uchi umenewo anawufula mu mkango wakufa. Tsopano Samsoni anapita ku nyumba kwa mtsikanayo. Ndipo kumeneko Samsoni anakonza phwando monga ankachitira anyamata. Makolo a mkwatibwiyo atamuona, anasankha anyamata makumi atatu kuti akhale naye. Samsoni anawawuza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi. Mukandiwuza tanthauzo lake asanathe masiku asanu ndi awiri aphwandowa, ndidzakupatsani zovala makumi atatu za bafuta ndi zina makumi atatu za tsiku la chikondwerero. Koma ngati simutha kundiwuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa zovala makumi atatu zabafuta ndi zina za tsiku la chikondwerero.” Iwo anamuyankha kuti, “Tiwuze mwambi wakowo tiwumve.” Iye anati, “Chakudya chinatuluka mu chinthu chodya chinzake; ndipo chozuna chinatuluka mu chinthu champhamvu.” Panapita masiku atatu anthuwo akulephera kumasulira mwambiwo. Tsiku lachinayi anthuwo anawuza mkazi wa Samsoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako kuti akuwuze tanthauzo la mwambiwu. Ngati sutero tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya abambo ako. Kodi unatiyitana kuti mudzatilande zinthu zathu?” Kenaka mkazi wa Samsoni anayamba kulira pamaso pake namuwuza kuti, “Inu mumandida ndipo simundikonda. Mwaphera anyamata a mtundu wathu mwambi, koma ine wosandiwuza tanthauzo lake.” Samsoni anamuyankha kuti, “Taona sindinawuze abambo kapena amayi anga, ndiye ndiwuze iweyo?” Mkaziyo anamulirira masiku onse asanu ndi awiri aphwandowo. Choncho pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuwuza tanthauzo lake popeza amamukakamiza. Ndipo mkaziyo anakawuza abale ake aja tanthauzo la mwambiwo. Pambuyo pake anthu a mu mzinda aja anamuwuza Samsoni pa tsiku lachisanu ndi chiwiri dzuwa lisanalowe kuti, “Chozuna nʼchiyani choposa uchi? Champhamvu nʼchiyani choposa mkango?” Samsoni anawawuza kuti, “Mukanapanda kutipula ndi ngʼombe yanga yayingʼono, simukanatha kumasulira mwambi wangawu.” Ndipo Mzimu wa Yehova unafika pa iye mwamphamvu. Choncho anatsikira ku Asikeloni naphako anthu makumi atatu, natenga zovala zawo za tsiku la chikondwerero napereka kwa anthu amene anamasulira mwambi wake. Kenaka anabwerera ku nyumba ya abambo ake ndi mkwiyo waukulu. Ndipo mkazi wa Samsoniyo anamukwatitsa kwa amene anali mnzake womuperekeza pa ukwati paja. Samsoni Abwezera Afilisti Patapita nthawi, mu nyengo yodula tirigu, Samsoni anatenga kamwana kambuzi ndipo anapita kukacheza kwa mkazi wake. Iye anati, “Ndikufuna kukalowa ku chipinda cha mkazi wanga.” Koma abambo a mkaziyo anamuletsa kutero. Abambo a mkaziyo anati, “Ine ndimaganiza kuti umamuda kwambiri nʼchifukwa chake ndinamupereka kwa mnzako. Kodi mngʼono wake uja sindiye wokongola kupambana iye? Ingotengani ameneyo mʼmalo mwake.” Samsoni anawawuza kuti, “Pano sindikhala wochimwa ndikawachita choyipa chachikulu Afilistiwa.” Choncho Samsoni anapita nakagwira nkhandwe 300 nazimangirira michira ziwiriziwiri ndipo pa fundo iliyonse ya michirayo anamangirira nsakali. Anayatsa nsakalizo kenaka ndi kuzitayira nkhandwe zija mʼminda ya tirigu ya Afilisti, ndipo zinatentha milu ya tirigu, ndi wosadula yemwe pamodzi ndi mitengo ya mpesa ndi ya olivi. Tsono Afilisti anayamba kufunsana kuti, “Ndani wachita izi?” Ena anati, “Ndi Samsoni mkamwini wa munthu wa ku Timna uja chifukwa Mtimunayo anatenga mkazi wake ndi kumupereka kwa mnzake.” Choncho Afilisti anapita kukatentha mtsikanayo pamodzi ndi abambo ake. Samsoni anawawuza kuti, “Ngati mumachita zangati zimenezi, ndiye ine sindileka mpaka nditakulipsirani.” Choncho Samsoni anamenyana nawo koopsa ndipo anapha ambiri a iwo. Kenaka anakalowa mʼphanga la Etamu, nakhala momwemo. Pambuyo pake Afilisti anakamanga misasa ya nkhondo mʼdziko la Yuda, ndi kuthira nkhondo mʼdera la Lehi. Anthu a fuko la Yuda anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwabwera kudzamenyana nafe?” Iwo anayankha kuti, “Tabwera kudzamanga Samsoni ndi kuti timuchite zofanana ndi zimene anatichita.” Ndipo anthu 3,000 a ku Yuda anapita ku phanga la Etamu, ndi kukamufunsa Samsoni kuti, “Kodi iwe sudziwa kuti ife amatilamulira ndi Afilisti? Tsono ndi chiyani chimene watichitachi?” Iye anayankha kuti, “Ine ndinachita zomwe iwo anandichita.” Iwo anati kwa iye, “Ife tabwera kuti tikumange ndi kukupereka kwa Afilisti.” Ndipo Samsoni anati, “Lonjezani mwa lumbiro kuti simundipha ndinu.” Iwo anamuyankha kuti, “Ayi, ife sitikupha. Koma tingokumanga ndi kukupereka mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho anamumanga ndi zingwe ziwiri zatsopano namutulutsa mʼphanga muja. Samsoni anafika ku Lehi, ndipo Afilisti anamuchingamira akufuwula. Nthawi yomweyo Mzimu wa Yehova unatsika pa iye mwamphamvu ndipo zingwe zimene anamumanga nazo zinasanduka ngati thonje lopsa mʼmoto, zinachita ngati zasungunuka nʼkuchoka mʼmanja mwake. Anapeza chibwano cha bulu amene anali atangofa kumene. Anachitola ndi kuphera nacho anthu 1,000. Ndipo Samsoni anati, “Ndi chibwano cha bulu, milu ndi milu ya anthu. Ndi chibwano cha bulu, ndapha anthu 1,000.” Atatsiriza kuyankhula, anataya chibwanocho, ndipo malowo anawatcha Ramati-Lehi. Pambuyo pake anamva ludzu kwambiri ndipo anayitana Yehova mopempha kuti, “Inu mwapatsa mtumiki wanu chipulumutso chachikulu chotere. Kodi tsopano ndife ndi ludzu ndi kugwidwa ndi anthu osachita mdulidwewa?” Pamenepo Mulungu anangʼamba nthaka ku Lehi, ndipo madzi anatuluka mʼdzenjemo. Samsoni anamwa madziwo, ndipo mphamvu zake zinabwerera nakhalanso monga analili. Choncho chitsimecho chinatchedwa Eni-Hakore, ndipo chilipobe ku Lehiko mpaka lero. Samsoni anatsogolera Israeli pa nthawi ya Afilisti kwa zaka makumi awiri. Samsoni ndi Delila Tsiku lina Samsoni anapita ku Gaza. Kumeneko anaonako mkazi wachiwerewere, ndipo analowa mu nyumba yake. Anthu a ku Gaza anawuzidwa kuti, “Samsoni ali kuno!” Choncho anthuwo anazungulira malowo, kumubisalira usiku wonse ku chipata cha mzindawo. Iwo anakhala chete usiku wonse namanena kuti, “Tidzamupha mmamawa.” Koma Samsoni anangogonako mpaka pakati pa usiku. Kenaka pakati pa usiku anadzuka nagwira zitseko za chipata cha mzinda ndi maferemu ake awiri, ndipo anazizula zonse pamodzi ndi mpiringidzo womwe. Anazisenza pa mapewa pake napita nazo pamwamba pa phiri loyangʼanana ndi Hebroni. Pambuyo pake, Samsoni anayamba kukonda mtsikana wina wa ku chigwa cha Soreki dzina lake Delila. Olamulira Afilisti anapita kwa mkaziyo ndipo anati, “Umunyengerere Samsoni kuti udziwe chinsinsi cha mphamvu zake zoopsazi, komanso ndi mmene ife tingamupambanire kuti timumange ndi kumugonjetsa. Ukatero aliyense wa ife adzakupatsa ndalama zasiliva 1,100.” Choncho Delila anati kwa Samsoni, “Inu tandiwuzani pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi ndi mmene anthu akhoza kukumangirani kuti akugonjetseni.” Samsoni anamuyankha kuti, “Ngati wina atandimanga ndi zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndidzafowoka ndi kusanduka ngati munthu wina aliyense.” Tsono atsogoleri a Afilisti aja anapita kwa mkazi uja namupatsa zingwe zisanu ndi ziwiri zatsopano zosawuma, ndipo mkaziyo anamanga nazo Samsoni. Nthawi imeneyo nʼkuti mkazi uja atayika anthu omubisalira mʼchipinda. Tsono anati kwa mwamuna wake, “Amuna anga, Afilisti aja afika!” Koma iye anangodula zingwe zija ngati mmene imadukira nkhosi ya chingwe ikamapsa. Choncho chinsinsi cha mphamvu zake sichinadziwike. Kenaka Delila anati kwa Samsoni, “Inu mwandipusitsa ndi kundiwuza zabodza. Chonde tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.” Iye anati, “Ngati aliyense atandimanga ine ndi zingwe zatsopano zimene sanazigwiritseko ntchito, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala monga munthu wina aliyense.” Choncho Delila anatenga zingwe zatsopano namumanga nazo. Kenaka anati “Amuna anga, Afilisti aja afikanso!” Nthawi iyi nʼkuti anthu omubisalira aja ali mʼchipinda chamʼkati. Koma iye anadulanso zingwe mʼmanja ake ngati akudula ulusi wa thonje. Ndipo Delila anati kwa Samsoni, “Mpaka tsopano mwakhala mukundipusitsa ndi kumandiwuza zabodza. Chonde, tandiwuzani mmene munthu angakumangireni.” Iye anayankha kuti, “Ngati njombi zisanu ndi ziwiri za kumutu kwanga utazilukira mu cholukira nsalu ndi kuchimanga molimbika ndi chikhomo, ndidzasanduka wofowoka ndi kukhala wofanana ndi munthu wina aliyense.” Choncho iye akugona, Delila analukira njombi za ku mutu kwa Samsoni mu cholukira nsalu nachimanga molimba ndi chikhomo. Pambuyo pake anati kwa Samsoni, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Tsono iye anadzuka ku tulo, nazula chikhomo chija ndipo njombi zinachoka mu cholukira chija. Tsono mkaziyo ananenanso kwa iye kuti, “Munganene bwanji kuti mumandikonda pamene mtima wanu suli pa ine? Aka ndi kachitatu mukundipusitsa ndipo simunandiwuze pamene pagona mphamvu zanu zoopsazi.” Tsono popeza anamupanikiza ndi mawu ake tsiku ndi tsiku ndi kumukakamiza, mtima wa Samsoni unatopa pafupi kufa. Choncho anamuwuza mkaziyo zonse za mu mtima mwake nati “Lumo silinapitepo pa mutu wanga chifukwa ndakhala ndili Mnaziri wopatulikira Mulungu chibadwire. Ngati nditametedwa mphamvu zanga zidzandichokera, ndidzasanduka wofowoka ndipo ndidzafanana ndi munthu wina aliyense.” Delila ataona kuti wamuwuza zonse za mu mtima mwake anatumiza uthenga kukayitana akuluakulu a Afilisti nati, “Bweraninso kamodzi kano kokha popeza wandiwululira zonse za mu mtima mwake.” Choncho akuluakulu a Afilisti aja anabwera ndi ndalama za siliva mʼmanja mwawo. Mkazi uja anagoneka Samsoni pa miyendo yake. Kenaka anayitana munthu wina ndipo anadzameta Samsoni njombi zisanu ndi ziwiri zija kumutu kwake. Pamenepo anayamba kufowoka, ndipo mphamvu zake zinamuchokera. Pambuyo pake mkaziyo anamuyitana kuti, “Amuna anga, Afilisti aja abwera!” Iye anadzuka kutuloko, naganiza kuti, “Ndituluka monga ndimachitira nthawi zonse ndi kudzimasula.” Koma sanadziwe kuti Yehova wamuchokera. Afilisti anamugwira ndipo anamukolowola maso. Kenaka anapita naye ku Gaza atamumanga ndi maunyolo achitsulo. Kumeneko anakhala wa pamphero mu ndende. Pambuyo pake tsitsi la pa mutu wake, monga linametedwa, linayambanso kumera. Imfa ya Samsoni Tsono atsogoleri a Afilisti anasonkhana kuti adzapereke nsembe yayikulu kwa Dagoni mulungu wawo ndi kukondwerera popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka Samsoni mdani wathu mʼmanja mwathu.” Anthuwo atamuona Samsoni, anayamba kutamanda mulungu wawo popeza ankanena kuti, “Mulungu wathu wapereka mdani wathu mʼmanja mwathu, ndiye amene anawononga dziko lathu, napha anthu athu ambirimbiri.” Ali mʼkati mosangalala, anthu aja amafuwula kuti, “Mutulutseni Samsoniyo kuti adzatisangalatse.” Choncho anamutulutsadi Samsoni mʼndende, ndipo anawasangalatsadi. Ndipo anamuyimiritsa pakati pa mizati. Pambuyo pake Samsoni anawuza mnyamata amene anamugwira dzanja kuti, “Ndilole kuti ndikhudze mizati imene yachirikiza nyumba yonseyi kuti ndiyitsamire.” Nthawi imeneyi nʼkuti nyumbayo ili yodzaza ndi anthu aamuna ndi aakazi. Olamulira onse a Afilisti anali momwemo, ndipo pamwamba pa nyumbayo panali anthu 3,000 aamuna ndi aakazi amene amaonerera Samsoni akusewera. Tsono Samsoni anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Ambuye anga, ndikumbukireni. Chonde ndilimbitseni nthawi yokha ino, inu Yehova, kuti ndiwabwezere Afilistiwa chifukwa cha maso anga awiri.” Choncho Samsoni anagwira mizati iwiri yapakati imene inkachirikiza nyumbayo. Anayitsamira ndi mphamvu zake zonse, dzanja lake lamanja ku mzati wina ndi dzanja lamanzere ku mzati winanso, ndipo Samsoni anati, “Ndife nawo pamodzi!” Nthawi yomweyo anakankha ndi mphamvu zake zonse ndipo mizati inagwera atsogoleri a Afilisti ndi anthu onse anali mʼmenemo. Tsono chiwerengero cha anthu amene Samsoni anapha pa nthawi ya imfa yake chinaposa cha iwo amene anawapha akanali ndi moyo. Kenaka abale ake ndi onse a pa banja la abambo ake anapita kukamutenga. Ndipo anakamuyika pakati pa Zora ndi Esitaoli mʼmanda a abambo ake, Manowa. Iye anatsogolera Israeli kwa zaka makumi awiri. Mafuno a Mika Munthu wina dzina lake Mika wochokera ku dziko la mapiri la Efereimu anawuza amayi ake kuti “Ndinamva inu mukutemberera munthu amene anaba ndalama zanu zasiliva 1,100. Ndalamazo zili ndi ine, ndinatenga ndine.” Pamenepo amayi akewo anati, “Yehova akudalitse mwana wanga!” Choncho Mika anabweza ndalama 1,100 za siliva kwa amayi ake, ndipo amayi akewo anati, “Ine ndapatulira Yehova ndalama za silivazi kuti mwana wanga aseme fano ndi kulikuta ndi siliva. Ndiye tsopano ndikubwezera ndalamazo.” Tsono Mika atabweza ndalama zija kwa amayi ake, iwo anatengapo ndalama za siliva 200 namupatsa mmisiri wosula siliva. Iye anakonza fano, nasungunula siliva uja ndi kulikutira fano lija. Ndipo Mika anayika fanolo mʼnyumba mwake. Mikayu anali ndi kachisi, ndipo anapanga efodi ndi mafano otchedwa terafimu. Anapatula mwana wake mmodzi kuti akhale wansembe. Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense amachita zomwe zinamukomera. Ku Betelehemu mʼdziko la Yuda kunali mnyamata wina amene anali wa fuko la Levi. Iyeyu anachoka mu mzinda wa Betelehemu uja ku Yuda kukafuna malo ena okhala. Akuyenda, anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ku nyumba ya Mika. Tsono Mika anamufunsa kuti, “Mukuchokera kuti?” Ndipo iye anayakha kuti, “Ndine Mlevi wochokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Ndikufunafuna malo okhala.” Tsono Mika anati kwa iye, “Khalani ndi ine. Mukhale ngati mlangizi wanga ndi wansembe, ndipo ine ndizikupatsani ndalama za siliva khumi pa chaka komanso zovala ndi zakudya.” Choncho Mleviyo anavomera kuti azikhala naye, ndipo mnyamatayo anakhala ngati mmodzi mwa ana ake aamuna. Pambuyo pake Mika anapatula Mleviyo ndipo mnyamatayu anakhala wansembe. Tsono ankakhala mʼnyumba ya Mika. Ndipo Mika anati, “Tsopano ndadziwa kuti Yehova adzandikomera mtima chifukwa Mleviyu ndiye wakhala wansembe wanga.” Fuko la Dani Likhala ku Laisi Masiku amenewo munalibe mfumu mu Israeli. Ndipo anthu a fuko la Dani amafunafuna malo okhalamo ngati cholowa chawo, chifukwa kufikira nthawi imeneyo anali asanalandire cholowa chawo pakati pa mafuko a Israeli. Choncho fuko la Dani linatumiza kuchokera ku mabanja awo onse anthu olimba mtima asanu. Anthuwa anachokera ku Zora ndi ku Esitaoli ndipo anatumidwa kukazonda ndi kuliyendera dzikolo. Anthu amenewa ankayimira fuko lonse la Dani. Anthuwa anawawuza kuti, “Pitani mukazonde dzikolo.” Anthuwa anafika ku dziko la mapiri la Efereimu ndi kupita ku nyumba ya Mika komwe anakagona. Ali ku nyumba ya Mika anazindikira mawu a mnyamata, Mlevi uja. Choncho anapita kwa iye namufunsa kuti, “Unabwera ndi ndani kuno? Nanga ukuchita chiyani ku malo ano? Komanso nʼchifukwa chiyani uli kuno?” Iye anawawuza zimene Mika anamuchitira ndipo anati, “Iye anandilemba ntchito ndipo ndine wansembe wake.” Kenaka iwo anati kwa iye, “Chonde tifunsire kwa Mulungu kuti tidziwe ngati ulendo wathuwu tiyende bwino.” Wansembeyo anawayankha kuti, “Pitani mu mtendere, Yehova ali ndi inu pa ulendo wanuwu.” Choncho anthu asanuwo ananyamuka ndipo anafika ku Laisi, kumene anaona kuti anthu ankakhala mwabata monga anthu a ku Sidoni. Anali anthu opanda chowavuta ndiponso aphee. Tsono popeza mʼdziko mwawo analibe chosowa, iwo anali a chuma. Anaonanso kuti anthuwo ankakhala kutali ndi Sidoni ndipo analibe ubale ndi wina aliyense. Ozonda dziko aja atabwerera kwa abale awo ku Zora ndi Esitaoli, abale awowo anawafunsa kuti, “Mwaonako zotani?” “Tiyeni tikamenyane nawo nkhondo popeza taliona dziko lawolo kuti ndi lachonde kwambiri. Kodi simuchitapo kanthu? Musachite mphwayi kupita mʼdzikomo ndi kukalilanda. Mukalowa, mukapeza anthu amene ali osatekeseka ndi dziko lalikulu. Yehova wakupatsani dziko limeneli. Malowo ngosasowa kanthu kalikonse kopezeka pa dziko lapansi.” Kenaka anthu 600 a fuko la Dani ananyamuka ku Zora ndi Esitaoli atanyamula zida za nkhondo. Tsono anakamanga msasa ku Kiriati-Yearimu mʼdziko la Yuda. Malowa ali kumadzulo kwa Kiriati-Yearimu. Ichi ndi chifukwa chake malowo akutchedwa Mahane Dani mpaka lero. Kuchokera kumeneko anapita ku dziko lamapiri la Efereimu ndipo anafika ku nyumba ya Mika. Anthu asanu amene anakazonda dziko la Laisi anati kwa abale awo, “Kodi mukudziwa kuti imodzi mwa nyumba izi muli efodi, mafano a mʼnyumba otchedwa terafimu, fano losema ndiponso fano lokuta ndi siliva? Ndiye mudziwe chochita.” Choncho anthuwa anapatuka napita ku nyumba ya Mika kumene mnyamata, Mlevi uja ankakhala ndipo anamufunsa za mmene zinthu zilili. Nthawi imeneyi nʼkuti anthu 600 a fuko la Dani aja atayima pa chipata atanyamula zida za nkhondo. Anthu asanu amene anakazonda dziko aja analowa ndi kukatenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba lotchedwa terafimu, ndi fano lokutidwa ndi siliva. Nthawiyi nʼkuti wansembe uja ndi anthu 600 okhala ndi zida za nkhondo aja ali chiyimire pa chipata. Anthuwo atalowa mʼnyumba ya Mika ndi kutenga fano losema, efodi, fano la mʼnyumba, ndi fano lokutidwa ndi siliva, wansembeyo anawafunsa kuti, “Kodi mukuchita chiyani?” Iwo anamuyankha kuti, “Khala chete usayankhule. Tsagana nafe ndipo udzakhala mlangizi wathu ndi wansembe wathu. Kodi si kwabwino kwa iwe kukhala wansembe wa fuko lonse la Israeli mʼmalo mokhala wansembe wa munthu mmodzi yekha?” Wansembeyo anakondwera ndipo anatenga efodi, fano la mʼnyumba ndi fano losema natsagana nawo. Choncho iwo anatembenuka nachoka, atatsogoza ana, zoweta ndi katundu wawo yense. Atayenda mtunda pangʼono kuchokera pa nyumba ya Mika, anthu amene amakhala pafupi ndi nyumba ya Mika anasonkhana kulondola a fuko la Dani aja, ndipo anawapeza. Atawafuwulira, a fuko la Dani aja anachewuka ndipo anafunsa Mika kuti, “Chavuta nʼchiyani kuti usonkhanitse anthu chotere?” Iye anayankha kuti, “Inu mwanditengera milungu imene ndinapanga pamodzi ndi wansembe nʼkumapita. Tsono ine ndatsala ndi chiyani? Ndiye inu mungafunse kuti chavuta nʼchiyani?” Anthu a fuko la Dani aja anayankha kuti, “Usayankhuleponso kanthu chifukwa anthu awa angapse mtima nakumenya ndipo iwe ndi banja lako lonse nʼkutayapo miyoyo yanu.” Choncho anthu a fuko la Dani anapitiriza ulendo wawo. Mika ataona kuti anthuwo anali amphamvu kuposa iye, anangotembenuka kubwerera kwawo. Anthu a fuko la Dani aja anatenga zinthu zimene Mika anapanga pamodzi ndi wansembe uja. Iwo anakafika ku Laisi kwa anthu a phee, osatekeseka aja ndipo anawathira nkhondo, nawapha ndi kutentha mzindawo ndi moto. Panalibe wowapulumutsa chifukwa anali kutali ndi Sidoni ndiponso sanali pa ubale ndi wina aliyense. Mzindawo unali mʼchigwa cha Beti-Rehobu. Anthu a fuko la Adaniwo anawumanganso mzindawo ndi kumakhalamo. Iwo anawutcha mzindawo Dani, kutengera dzina la kholo lawo Dani, amene anali mwana wa Israeli, ngakhale kuti mzindawo poyamba unali Laisi. Anthu a fuko la Dani anayimiritsa fano losema lija. Yonatani mwana wa Geresomu, mwana wa Mose pamodzi ndi ana ake onse anakhala ansembe a fuko la Dani mpaka pa tsiku la ukapolo wa dzikolo. Choncho anthu a fuko la Dani ankapembedza fano limene Mika anapanga nthawi yonse pamene nyumba ya Mulungu inali ku Silo. Mlevi ndi Mzikazi Wake Pa nthawi imeneyo ku Israeli kunalibe mfumu. Mlevi wina ankakhala kutali ku dziko lamapiri la Efereimu. Iyeyu anatenga mzikazi wa ku Betelehemu, mʼdziko la Yuda. Tsiku lina mzikazi uja anakwiyira mwamuna wake ndipo anamuchokera kupita kwa abambo ake ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Anakakhala kumeneko miyezi inayi. Mwamuna wake anamulondola kuti akayankhule naye mofatsa kumupempha kuti abwerere. Iye anali ndi antchito ake ndi abulu ake awiri. Anafika ku nyumba kwa mkazi uja ndipo iye anamulowetsa mʼnyumba ya abambo ake. Abambo aja atamuona mnyamata uja anamulandira mwachimwemwe. Mpongozi wake, yemwe anali abambo a mtsikanayo, anamupempha kuti aswere. Choncho anakhalako masiku atatu. Ankadya, kumwa ndi kugona komweko. Tsiku lachinayi anadzuka mʼmamawa kukonzekera kuti azipita kwawo, koma abambo ake a mtsikanayo anawuza mkamwini wawo uja kuti, “Yambani mwadya chakudya, ndipo kenaka mutha kupita.” Choncho onse awiri anakhala pansi ndi kudya ndi kumwa pamodzi. Atadya, abambo a mtsikanayo anati, “Chonde mugonenso konkuno musangalale.” Ndipo pamene mwamunayo anakonzeka kuti azipita, apongozi ake anamuwumirizanso kuti asapite. Choncho anagona komweko usiku umenewo. Mmawa wa tsiku lachisanu, atadzuka kuti azipita abambo ake a mtsikanayo anamuwuza kuti, “Yambani mwadya chakudya ndipo mutandale mpaka madzulo.” Choncho awiriwo anadya pamodzi. Pambuyo pake munthu uja pamodzi ndi mzikazi wake ndiponso mtumiki anakonzeka kuti azipita. Koma abambo a mtsikana uja anatinso kwa iye, “Onani tsopano kukuda. Gonani konkuno pakuti tsiku latha kale. Gonani ndipo musangalale. Mawa mudzuka mʼmamawa ndi kumapita kwanu.” Koma munthuyo sanafune kugonanso tsiku limenelo. Choncho ananyamuka kumapita, ndipo anakafika ku malo oyangʼanana ndi Yebusi (ndiye kuti Yerusalemu). Iyeyo anali atatenga abulu ake awiri okhala ndi zokhalira zake, ndipo mzikazi wake uja anali naye limodzi. Akuyandikira ku Yebusi nʼkuti kutada ndithu. Tsono mtumiki uja anawuza mbuye wake kuti, “Tiyeni, tipatukire ku mzinda wa Ayebusiwa ndipo tigone.” Mbuye wake anamuyankha kuti, “Ayi, tisapatukire ku mzinda wa alendo, anthu amene sali Aisraeli. Koma tipitirire mpaka ku Gibeya.” Tsono anamuwuza mtumiki wake uja kuti, “Tiye tipite ku amodzi a malo awa, ku Gibeya kapena ku Rama ndipo tikagone kumeneko.” Choncho nayenda ulendo wawo, ndipo dzuwa linawalowera akuyandikira ku Gibeya mʼdziko la Benjamini. Ndipo anapatukira kumeneko kuti alowe mu mzinda wa Gibeya kukagona usiku umenewo. Anakalowa mu mzindamo ndi kukakhala pabwalo popeza panalibe munthu amene anawalandira ku nyumba kwake kuti akagone. Pambuyo pake anangoona munthu wina wokalamba akuchokera ku ntchito ya ku munda kwake madzulo. Iyeyu anali wa ku dziko la mapiri ku Efereimu, koma ankakhala ku Gibeya. Koma anthu a kumeneko anali a fuko la Benjamini. Munthu wokalamba uja anakweza maso ndipo anaona munthu wa paulendo uja atakhala pabwalo la mzindawo, ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mukupita kuti? Nanga mukuchokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Tikuchokera ku Betelehemu ku dziko la Yuda ndipo tikupita kutali ku dziko lamapiri la Efereimu kumene ndimakhala. Ndinapita ku Betelehemu mʼdziko la Yuda ndipo tsopano ndikubwerera kwathu. Koma palibe aliyense amene wanditengera ku nyumba yake. Tili ndi udzu ndi chakudya cha abulu athu. Tilinso ndi buledi ndi vinyo wokwanira ifeyo: ine, mdzakazi wanuyu, ndi mtumiki amene ali nafeyu. Palibe chimene tikusowa.” Munthu wokalambayo anati, “Mtendere ukhale nanu. Ine ndikuthandizani pa zosowa zanu zonse, koma musagone pabwalo usiku uno.” Choncho anapita nawo ku nyumba yake, ndipo anawapatsa abulu ake chakudya. Alendo aja anasamba mapazi awo, nalandira chakudya ndi chakumwa. Pamene ankadya mosangalala, anangoona anthu ena achabechabe a mu mzindawo azungulira nyumba ija nʼkumamenya chitseko. Tsono anawuza mwini nyumbayo, munthu wokalamba uja kuti, “Mutulutse munthu amene wabwera mʼnyumba yakoyu kuti tigone naye.” Koma mwini nyumba uja anatuluka ku bwalo nawawuza kuti, “Ayi, abale anga musachite zoyipa zotere. Popeza munthu uyu walowa mʼnyumba mwanga muno, musachite chinthu chonyansa chotere. Onani, pano pali mwana wanga wamkazi wosadziwa mwamuna pamodzi ndi mzikazi wa mlendoyu. Ndikutulutsirani amenewa tsopano ndipo atengeni ndi kuchita nawo chomwe chikukomerani. Koma musachite chinthu chonyansa ndi munthuyu.” Koma anthuwo sanafune kumumvera. Choncho mlendo uja anagwira mzikazi wake namutulutsa kuja kumene kunali iwo. Tsono iwowo anagona naye ndi kuchita naye zonyansa usiku wonse mpaka mmawa. Mʼbandakucha anamulola kuti apite. Ndipo mmawa kukucha mzikazi uja anabwerera nakagwa pansi pa khomo pa nyumba imene mwamuna wake anali, ndipo anakhala pomwepo mpaka kunayera. Mwamuna wake anadzuka mʼmamawa, natsekula chitseko cha nyumba kuti atuluke ndi kumapita. Koma anangoona mzikazi wake uja ali thapsa pa khomo la nyumbayo, manja ake ali pa khonde. Iye anati kwa mkaziyo, “Dzuka tizipita.” Koma sanayankhe kanthu. Kenaka anamukweza pa bulu wake ndipo ananyamuka kumapita kwawo. Atafika ku nyumba yake, anatenga mpeni, nagwira mzikazi wake uja ndi kuduladula thupi lake nthuli khumi ndi ziwiri. Kenaka anazitumiza ku zigawo zonse za Israeli. Aliyense amene anaona zimenezi ankanena kuti, “Zoterezi sizinaonekepo kuyambira pamene Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ganizirani bwino chinthu chimenechi ndipo tiwuzeni zoyenera kuchita!” Aisraeli Achita Nkhondo ndi Fuko la Benjamini Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dziko la Dani mpaka ku Beeriseba ndiponso ku dziko la Giliyadi ananyamuka ngati munthu mmodzi nakasonkhana pamaso pa Yehova ku Mizipa. Atsogoleri a anthu onse ndi a mafuko onse Aisraeli anali nawo pa msonkhano wa anthu a Mulungu. Onse pamodzi analipo asilikali oyenda pansi 400,000 atanyamula malupanga. Anthu a fuko la Benjamini anali atamva kuti Aisraeli apita ku Mizipa. Tsono Aisraeli anati, “Tiwuzeni, zinthu zoyipa izi zinachitika bwanji.” Choncho Mlevi uja, mwamuna wa mkazi wophedwa uja anayankha nati, “Ine ndinapita ku Gibeya mʼdziko la Benjamini pamodzi ndi mzikazi wanga kuti tikagone kumeneko. Usiku anthu a ku Gibeya anandiwukira, nazinga nyumba munali ine. Ankafuna kundipha ndipo anagona ndi mzikazi wanga momukakamiza mpaka anafa. Ine ndinatenga mzikazi wangayo ndi kumudula nthulinthuli ndikuzitumiza kwa fuko lililonse la Aisraeli. Anthu amenewa, zedi achita chinthu chonyansa kwambiri mʼdziko lino la Israeli. Ndi zimenezotu inu Aisraeli nonse; yankhulaponi mawu ndi kupereka maganizo anu.” Anthu onse anayimirira ngati munthu mmodzi nanena kuti, “Palibe mmodzi wa ife amene apite ku nyumba kwake. Palibe amene abwerere ku nyumba kwake. Koma tsopano chimene ife tichite ndi dziko la Gibeya ndi ichi: Tidzapita kukamenyana nawo potsatira zimene maere anene. Mʼmafuko onse a Aisraeli tidzasankha anthu khumi pa anthu 100 aliwonse: ndiye kuti anthu 100 pa anthu 1,000 aliwonse kapena anthu 1,000 pa anthu 10,000 aliwonse. Anthu amenewa adzasonkhanitsa zakudya za ankhondo, ndipo ankhondowo adzapita kukalipsira anthu a ku Geba mʼdziko la Benjamini chifukwa chochita chinthu chonyansa chotere mʼdziko la Israeli.” Choncho anthu a ku Israeli anasonkhana pamodzi nagwirizana chimodzi, kukalimbana ndi mzindawo. Mafuko a Israeli anatumiza anthu kwa fuko lonse la Benjamini kukafunsa kuti, “Kodi zoyipa zachitika pakati panuzi ndi zotani? Tsono tikuti mutipatse anthu achabechabe a ku Gibeya kuti tiwaphe kuti tichotse chinthu choyipachi mʼdziko la Israeli.” Koma fuko la Benjamini silinafune kumvera zimene ananena Aisraeli anzawo. Mʼmalo mwake, Abenjaminiwo anatuluka mʼmizinda yawo ku Gibeya kukamenyana ndi Aisraeli. Tsiku limenelo Abenjamini anasonkhanitsa kuchokera ku mizinda yawo ankhondo 26,000 amalupanga awo, osawerengera anthu ena 700 a ku Gibeya amene anasankhidwa. Mwa onsewa panali ankhondo 70 amanzere amene aliyense anali wodziwa kulasa ngakhale tsitsi limodzi ndi mwala osaphonya. Aisraeli, kupatula fuko la Benjamini, anasonkhanitsa anthu 400,000 a malupanga, onse odziwa bwino nkhondo. Ndipo Aisraeli ananyamuka kupita ku Beteli kukafunsira kwa Mulungu. Iwo anati, “Ndani mwa ife amene angayambe kukamenyana ndi fuko la Benjamini?” Yehova anayankha kuti, “Fuko la Yuda ndilo liyambe.” Mmawa mwake Israeli ananyamuka nakamanga msasa moyangʼanana ndi Gibeya. Aisraeli anapita kukachita nkhondo ndi fuko la Benjamini ndipo anandandalika ankhondo awo moyangʼanana ndi Gibeya. A fuko la Benjamini anatuluka ku Gibeya ndipo tsiku limenelo anapha Aisraeli 22,000 ku nkhondoko. Koma ankhondo a Israeli analimbikitsananso mtima ndipo anasonkhanitsanso kachiwiri ankhondo awo pa malo pamene anawandandalika poyamba paja. Aisraeli anapita kukalira pamaso pa Yehova mpaka madzulo. Iwo anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukamenyana ndi a fuko la Benjamini abale athu?” Yehova anayankha kuti, “Pitani mukalimbane nawo.” Ndipo Aisraeli anayandikiranso pafupi ndi fuko la Benjamini tsiku lachiwiri lake kuti amenyane nawo. Pa tsiku lachiwiri lomwelo Abenjamini anatulukanso mu mzinda wa Gibeya ndipo anaphanso ankhondo 18,000. Onse amene anawaphawo anali odziwa kugwiritsa ntchito bwino malupanga. Tsono Aisraeli onse, gulu lonse la ankhondo, anapita ku Beteli kukalira pamaso pa Yehova. Anakhala pansi nasala zakudya tsiku lonse mpaka madzulo. Anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. Bokosi la Chipangano cha Yehova linali kumeneko. Finehasi mwana wa Eliezara mwana wa Aaroni ndiye ankatumikira nthawi imeneyo. Tsono Aisraeli anafunsa Yehova kuti, “Kodi tipitenso kukachita nkhondo ndi mʼbale athu Abenjamini, kapena ayi?” Yehova anayankha kuti, “Pitaninso chifukwa mawa ndidzawapereka mʼmanja mwanu.” Choncho Aisraeli anayika anthu obisalira mozungulira Gibeya. Tsiku lachitatu anapita kukamenyana ndi Benjamini ndipo anayika ankhondo mʼmalo mwawo kuti amenyane ndi Gibeya monga anachitira poyamba. Abenjamini anatuluka kukamenyana nawo anthuwo ndipo anapita kutali ndi mzindawo. Iwo anayamba kupha Aisraeli monga poyamba paja, kotero kuti anapha anthu pafupifupi makumi atatu. Mitembo ya ena inali mu misewu yayikulu yopita ku Beteli ndi ku Gibeya, ndipo ina inali kwina poyera. Abenjamini ankanena kuti, “Tikuwagonjetsa monga poyamba.” Koma Aisraeli ankanena kuti, “Tiyeni tithawe kuti apite ku msewu chapatali ndi mzinda wawo.” Choncho Aisraeli onse anachoka mʼmalo mwawo ndi kukandanda ku Baala-Tamara, ndipo Aisraeli obisalira aja anatuluka mʼmalo awo kummawa kwa Geba. Aisraeli osankhidwa 10,000 ndiwo anabwera kudzalimbana ndi mzinda wa Gibeya. Nkhondoyo inafika poyipa kwambiri mwakuti Abenjamini samadziwa kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera. Tsono Yehova anagonjetsa Abenjamini pamaso pa Israeli motero kuti Aisraeli anapha ankhondo a Abenjamini 25,100 tsiku limenelo. Choncho Abenjamini anaona kuti agonjetsedwa. Paja Aisraeli anathawa fuko la Benjamini chifukwa ankadalira anthu amene anawayika kuti abisalire mzinda wa Gibeya. Tsono anthu amene anabisala aja anachita changu kuwuthira nkhondo mzinda wa Gibeyawo. Ndipo anapha anthu onse a mu mzindawo ndi lupanga. Chizindikiro chimene Aisraeli anapangana ndi anthu obisalira aja chinali chakuti obisalira aja akangofukiza utsi wambiri ngati mtambo mu mzindamo, ndiye kuti Aisraeli enawo abwerere ku nkhondo. Pa nthawiyo nʼkuti Abenjamini atayamba kale kumenya Aisraeliwo kwambiri ndi kupha pafupifupi anthu makumi atatu. Ndipo iwo ankanena kuti, “Ndithu tawapha monga poyamba paja.” Koma pamene utsi wa chizindikiro uja unayamba kukwera tolotolo mmwamba kuchoka mu mzindamo, Abenjamini anayangʼana mʼmbuyo ndipo anangoona utsi mu mzinda onse uli tolotolo kukwera mmwamba. Kenaka Aisraeli anabwerera ndipo Abenjamini anachita mantha, chifukwa anaona kuti zoopsa zili pafupi kuwagwera. Choncho anathawa pamaso pa Aisraeli kudzera njira ya ku chipululu, koma nkhondo inawapeza. Ndipo anaphedwa kumeneko ndi Aisraeli amene anachokera mu mzindamo. Anawazungulira Abenjaminiwo, nawathamangitsa ndi kuwagonjetseratu osawachitira chifundo mpaka ku dera la kummawa kwa Gibeya. Abenjamini 18,000 olimba mtima anaphedwa. Koma ena anatembenuka nathawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni. Mwa iwowa Aisraeli anapha Abenjamini 5,000 mʼmisewu yayikulu. Anawapitikitsabe Abenjaminiwo mpaka kufika ku Gidomu ndi kuphanso ena 2,000. Pa tsiku limenelo Abenjamini olimba mtima okhala ndi malupanga okwana 25,000 anafa. Koma anthu 700 anabwerera ndi kuthawira ku chipululu ku thanthwe la Rimoni kumene anakhalako miyezi inayi. Aisraeli anabwerera kukamenyana ndi Abenjamini otsala ndi kuwapha ndi lupanga kuphatikizapo ziweto ndi zonse anali nazo. Ndipo anayatsa moto mizinda yonse anayipeza. Akazi a Abenjamini Aisraeli anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe mmodzi wa ife adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.” Anthu anapita ku Beteli kumene anakakhala pansi pamaso pa Mulungu mpaka madzulo. Iwo anakweza mawu nalira kwambiri. Iwo ankanena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli, nʼchifukwa chiyani izi zachitika mʼdziko la Israeli kuti lero fuko limodzi lisowe mu Israeli?” Mmawa mwake anthu anadzuka namanga guwa lansembe ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka Aisraeli anafunsa kuti, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Israeli sanafike ku msonkhano wa Yehova?” Anatero chifukwa anachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene alephere kupita ku Mizipa ndi kuti woteroyo ayenera kuphedwa. Tsono Aisraeli anamva chisoni chifukwa cha abale awo, Abenjamini. Iwo anati, “Lero fuko limodzi lachotsedwa mu Israeli. Kodi tingawapezere bwanji anthu otsalawa akazi woti awakwatire? Paja ife tinalumbira kwa Yehova kuti sitidzapereka ana anthu aakazi kuti awakwatire. Kenaka anafunsa kuti, ‘Kodi mu fuko la Israeli ndani amene sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?’ ” Tsono panapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wochokera ku Yabesi Giliyadi amene anapita ku msonkhano ku misasa kuja. Pamene anthu anawerengana anangoona kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi palibe. Choncho msonkhano unatumiza anthu ankhondo 12,000 ndi kuwalamula kuti, “Mukaphe anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi, kuphatikizapo akazi ndi ana.” Izi ndi zimene mukachite. “Mukaphe mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense amene anadziwapo mwamuna.” Iwo anapeza atsikana 400 pakati pa anthu okhala mu Yabesi Giliyadi amene anali asanadziwepo mwamuna ndipo anabwera nawo ku misasa ku Silo mʼdziko la Kanaani. Kenaka msonkhano wonse unatumiza uthenga kwa Abenjamini amene ankakhala ku thanthwe la Rimoni kuwawuza kuti nkhondo yatha. Choncho Abenjamini anabwera nthawi imeneyo ndipo Aisraeli anawapatsa akazi a ku Yabesi Giliyadi amene sanaphedwe. Koma sanapezeke owakwanira. Aisraeli anamvera chisoni Abenjamini, chifukwa Yehova anachita ngati waligwerula dzino fuko la Israeli. Choncho akuluakulu a msonkhano anati, “Kodi tikawapezera kuti akazi anthu otsalirawa kuti awakwatire popeza kuti akazi a fuko la Benjamini anaphedwa?” Iwo anati, “Abenjamini amene anapulumukawa ayenera kukhala ndi zidzukulu, kuti mtundu wa Israeli usafafanizike. Ife sitingathe kuwapatsa ana anthu aakazi kuti akwatire. Paja tinalumbira kuti, ‘Akhale wotembereredwa aliyense amene adzapereka mwana wake wamkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini kuti akwatire.’ Ndipo anati, ‘Paja ku Silo kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Yehova. Tsono Silo ali kumpoto kwa Beteli, kummawa kwa msewu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kummwera kwa Lebona.’ ” Choncho anawalamulira Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale mʼminda ya mpesa ndipo mukakhale tcheru. Ana aakazi a ku Silo akadzatulukira kudzavina nawo magule, pomwepo inu mutuluke minda ya mpesa ndi kukawagwira aliyense wake ndi kupita nawo ku dziko la Benjamini. Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ” Abenjamini anachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja anagwirapo ena, malingana ndi chiwerengero chawo, nawatenga kuti akhale akazi awo. Kenaka ananyamuka kubwerera ku dziko la kwawo, nakamanganso mizinda yawo ndi kumakhalamo. Pambuyo pake Aisraeli anachoka kumeneko ndi kubwerera kwawo, ku mafuko ndi ku mabanja awo, aliyense ku dera la cholowa chake. Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense ankangochita zimene zomukomera yekha.