- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
YAKOBO
Kalata ya Yakobo
Yakobo
Yak
KALATA YA
YAKOBO
Yakobo, mtumiki wa Mulungu ndi wa Ambuye Yesu Khristu,
kulembera mafuko khumi ndi awiri obalalikana ku mayiko osiyanasiyana.
Landirani moni.
Masautso ndi Mayesero
Abale, muchiyese ngati chimwemwe chenicheni nthawi zonse pamene mukukumana ndi mayesero amitundumitundu. Inu mukudziwa kuti kuyesedwa kwa chikhulupiriro chanu kumabweretsa chipiriro. Chipiriro chiyenera kugwira ntchito yake kuti mukhale okhwima ndi angwiro, osasowa kanthu kalikonse. Ngati wina pakati panu akusowa nzeru, apemphe kwa Mulungu amene amapereka kwa onse mwaulere ndi mosatonzera, ndipo adzapatsidwa. Koma pamene mupempha, muyenera kukhulupirira osakayika, chifukwa amene amakayika ali ngati mafunde pa nyanja amene amawinduka nakankhika ndi mphepo. Munthu wotere asayembekezere kulandira kalikonse kuchokera kwa Ambuye. Iyeyu ndi munthu wa mitima iwiri, wosakhazikika pa zimene akuchita.
Abale omwe ndi anthu wamba anyadire pamene akwezedwa. Koma olemera anyadire pamene atsitsidwa, chifukwa adzatha ngati duwa lakuthengo. Pakuti dzuwa limatuluka nʼkutentha kwake, ndipo limafotetsa zomera. Duwa lake limathothoka ndipo kukongola kwake kumatheratu. Momwemonso munthu wachuma adzazimirira ngakhale atamachitabe malonda ake.
Wodala ndi munthu amene amapirira mʼmayesero, chifukwa akapambana adzalandira chipewa cha ulemerero chimene Mulungu analonjeza anthu amene amamukonda.
Munthu akayesedwa asanene kuti, “Mulungu akundiyesa.” Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi choyipa kapena Iyeyo kuyesa munthu aliyense. Koma munthu aliyense amayesedwa akakokedwa ndi zilakolako zake zoyipa ndi kukopedwa nazo. Pamenepo, chilakolako chikakula chimabala tchimo; ndipo tchimo likakhwima limabereka imfa.
Musanyengedwe abale anga okondedwa. Mphatso iliyonse yabwino ndi yangwiro imachokera kumwamba, kwa Atate mwini kuwala, amene sasintha ngati mthunzi woyendayenda. Iye anasankha kutibereka ife kudzera mʼmawu a choonadi, kuti pakati pa zolengedwa zake zonse, tikakhale ngati zipatso zoyamba.
Kumva ndi Kuchita
Abale anga okondedwa, gwiritsitsani mawu awa: munthu aliyense azifulumira kumva, koma asamafulumire kuyankhula, ndipo asamafulumirenso kupsa mtima. Pakuti mkwiyo wa munthu subweretsa chilungamo chimene amafuna Mulungu. Choncho chotsani chizolowezi choyipa ndi khalidwe loyipa pakati panu, ndipo modzichepetsa landirani mawu amene anadzalidwa mwa inu, amene akhoza kukupulumutsani.
Musamangomvetsera chabe mawu, ndi kumadzinyenga nokha. Chitani zimene mawuwo amanena. Munthu aliyense amene amangomva mawu koma osachita zimene mawuwo amanena, ali ngati munthu amene amayangʼana nkhope yake pa galasi. Akadziyangʼana amachoka, nthawi yomweyo nʼkuyiwala mmene akuonekera. Koma munthu amene amayangʼana mwachidwi lamulo langwiro limene limapatsa ufulu ndi kupitiriza kutero, osayiwala chimene wamva koma kuchita adzadalitsika pa zimene amachita.
Ngati wina amadziyesa ngati ndi wachipembedzo, koma chonsecho saletsa lilime lake, amadzinyenga yekha ndipo chipembedzo chakecho ndi cha chabechabe. Chipembedzo chimene Mulungu Atate athu amachivomereza kuti ndi changwiro ndi chopanda zolakwika ndi ichi: kusamalira ana amasiye ndi akazi amasiye pa mavuto awo, ndi kudzisunga bwino kuopa kudetsedwa ndi dziko lapansi.
Kuchita Tsankho Nʼkosaloledwa
Abale anga, okhulupirira Yesu Khristu waulemerero, musaonetse tsankho. Tangoganizirani, pakati panu patabwera munthu atavala mphete yagolide ndi zovala zapamwamba, ndipo winanso wosauka nʼkulowa atavala sanza. Ngati musamala kwambiri munthu wovala bwinoyu uja, nʼkumuwuza kuti, “Khalani pa mpando wabwinowu,” koma wosauka uja nʼkumuwuza kuti, “Ima apo,” kapena “Khala pansi pafupi ndi chopondapo mapazi angawa,” kodi simunachite tsankho pakati panu ndi kukhala oweruza a maganizo oyipa?
Tamverani abale anga okondedwa, kodi Mulungu sanasankhe amene dziko lapansi limawaona ngati amphawi kuti akhale olemera mʼchikhulupiriro ndi kulowa ufumu umene Iye analonjeza kwa amene amamukonda? Koma mwakhala mukunyoza amphawi. Kodi si anthu olemerawa amene akukudyerani masuku pamutu? Si anthu amenewa amene amakukokerani ku bwalo la milandu? Kodi si omwewa amene amachita chipongwe dzina la wolemekezeka, limene inu mumatchulidwa?
Ngati musungadi lamulo laufumu lija lopezeka mʼMalemba lakuti, “Konda mnansi wako monga iwe mwini,” ndiye kuti mukuchita bwino. Koma mukamaonetsa tsankho mukuchimwa, ndipo ndinu wochimwa monga wophwanya lamulo. Pakuti amene amasunga Malamulo onse, akangophwanya fundo imodzi yokha, waphwanya Malamulo onse. Pakuti amene anati “Usachite chigololo” ndi yemweyonso anati “Usaphe.” Ngati suchita chigololo koma umapha, ndiwe wophwanya Malamulo.
Muziyankhula ndi kuchita zinthu monga anthu amene mudzaweruzidwe ndi lamulo limene limapereka ufulu, chifukwa munthu woweruza mopanda chifundo, nayenso adzaweruzidwa mopanda chifundo. Chifundo chimapambana pa chiweruzo.
Chikhulupiriro ndi Ntchito Zabwino
Abale anga, phindu lake nʼchiyani ngati munthu anena kuti ali ndi chikhulupiriro koma chopanda ntchito zabwino? Kodi chikhulupiriro choterechi chingamupulumutse? Tangoganizirani, mʼbale kapena mlongo amene ali ndi usiwa, ndipo alibe chakudya cha tsiku ndi tsiku. Ngati mmodzi wa inu amuwuza kuti, “Pita ndi mtendere, ukafundidwe ndipo ukakhute,” koma osamupatsa zimene akuzisowa, phindu lake nʼchiyani pamenepa? Chomwechonso, chikhulupiriro chokha chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
Koma wina anganene kuti, “Inuyo muli ndi chikhulupiriro koma ine ndili ndi ntchito zabwino.”
Onetsani chikhulupiriro chanu chopanda ntchito zabwino ndipo ineyo ndidzakuonetsani chikhulupiriro changa pochita ntchito zabwino. Mumakhulupirira kuti kuli Mulungu mmodzi yekha. Mumachita bwino. Komatu ngakhale ziwanda zimakhulupirira zimenezi ndipo zimanjenjemera ndi mantha.
Munthu wopusa iwe, kodi ukufuna umboni woti chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino nʼchakufa? Kodi Abrahamu kholo lathu sanatengedwe kukhala wolungama chifukwa cha zimene anachita pamene anapereka mwana wake Isake pa guwa lansembe? Tsono mukuona kuti chikhulupiriro chake ndi ntchito zabwino zinkachitika pamodzi, ndipo chikhulupiriro chake chinasanduka chenicheni chifukwa cha ntchito zake zabwino. Ndipo Malemba akunena kuti, “Abrahamu anakhulupirira Mulungu ndipo anatengedwa kukhala wolungama,” ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. Tsono mukuona kuti munthu amasanduka wolungama ndi ntchito zabwino osati ndi chikhulupiriro chokha ayi.
Nʼchimodzimodzinso, kodi wadama uja, Rahabe, sanasanduke wolungama chifukwa cha zomwe anachita pamene anapereka malo ogona kwa azondi aja ndi kuwathawitsira mbali ina? Monga thupi lopanda mzimu ndi lakufa, chomwechonso chikhulupiriro chopanda ntchito zabwino ndi chakufa.
Za Lilime
Abale anga, ambiri musakhale aphunzitsi chifukwa mumadziwa kuti aphunzitsife tidzaweruzidwa mowuma kuposa anthu ena onse. Tonsefe timapunthwa mʼnjira zambiri. Ngati wina salakwa poyankhula, ameneyo ndi munthu wangwiro, wodziwa kuyangʼanira bwino thupi lake lonse.
Tikayika tizitsulo mʼkamwa mwa akavalo kuti atimvere, timatha kuwongolera thupi lake lonse. Taonani sitima zapamadzi. Ngakhale ndi zazikulu kwambiri ndipo zimakankhidwa ndi mphepo yamphamvu, zimawongoleredwa ndi tsigiro lalingʼono kulikonse kumene woyendetsayo akufuna kupita. Momwemonso, lilime ndi kachiwalo kakangʼono ka thupi koma limadzitama kuti nʼkuchita zikuluzikulu. Tangoganizirani za nkhalango yayikulu imene ingapse ndi kalawi kamoto koyamba mochepa. Lilime nalonso ndi moto, dziko la zoyipa pakati pa ziwalo za thupi. Limawononga munthu yense wathunthu. Limayika zonse za moyo wake pa moto, ndipo moto wake ndi wochokera ku gehena.
Mitundu yonse ya nyama, ya mbalame, ya zokwawa ndi ya zolengedwa za mʼnyanja, zikuwetedwa ndipo munthu wakhala akuziweta, koma palibe munthu amene angaweta lilime. Lilime ndipo silitha kupuma, ndi lodzaza ndi ululu wakupha.
Ndi lilime lomwelo timatamanda Ambuye ndi Atate athu, komanso ndi lilime lomwelo timalalatira anthu, amene anapangidwa mʼchifanizo cha Mulungu. Mʼkamwa momwemo mutuluka matamando ndi kulalata. Abale anga, zisamatero ayi. Kodi madzi abwino ndi a mchere angatuluke pa kasupe mmodzi? Abale anga, kodi mtengo wa mkuyu nʼkubala mphesa, kapena mtengo wampesa nʼkubala nkhuyu? Kasupe wa madzi a mchere sangatulutsenso madzi abwino.
Mitundu Iwiri ya Nzeru
Ndani mwa inu amene ndi wanzeru ndi womvetsa zinthu? Mulekeni aonetse ndi makhalidwe ake abwino kuti nzeru ndiye zikutsogolera kudzichepetsa kwake ndi zochita zake Koma ngati muli ndi mtima wakaduka ndi odzikonda, musadzitamandire kapena kukana choonadi. “Nzeru” zotere sizochokera kumwamba koma ndi za mʼdziko lapansi, si zauzimu koma ndi za ziwanda. Pakuti pamene pali kaduka ndi kudzikonda pomweponso pamakhala chisokonezo ndi zochitika zoyipa zonse.
Koma nzeru imene imachoka kumwamba, poyamba ndi yangwiro, ndi yokonda mtendere, yoganizira za ena, yogonjera, yodzaza ndi chifundo ndi chipatso chabwino, yosakondera ndi yoona mtima. Anthu amtendere amene amadzala mtendere amakolola chilungamo.
Kugonjera Mulungu
Nʼchiyani chimene chimayambitsa ndewu ndi mapokoso pakati panu? Kodi sizichokera ku zilakolako zimene zimalimbana mʼkati mwanu? Mumalakalaka zinthu koma simuzipeza, choncho mumapha. Mumasirira zinthu koma simutha kuzipeza zimene mukufuna, choncho mumakangana ndi kumenyana. Mulibe zinthuzo chifukwa simupempha kwa Mulungu. Koma ngakhale mumapempha simulandira, chifukwa mumapempha ndi zolinga zoyipa. Mumapempha kuti muzigwiritse ntchito pa zokusangalatsani nokha.
Inu anthu achigololo, kodi simukudziwa kuti kuchita ubwenzi ndi dziko lapansi ndi kudana ndi Mulungu? Choncho, aliyense wosankha kukhala bwenzi la dziko lapansi amasanduka mdani wa Mulungu. Kapena mukuganiza kuti Malemba amanena popanda chifukwa kuti Mulungu amafunitsitsa mwansanje mzimu umene Iye anayika kuti uzikhala mwa ife? Koma amatipatsa chisomo chochuluka. Nʼchifukwa chake Malemba amati,
“Mulungu amatsutsa odzikuza,
koma apereka chisomo kwa odzichepetsa.”
Dziperekeni nokha kwa Mulungu. Mukaneni Mdierekezi ndipo adzakuthawani. Sendezani kufupi ndi Mulungu ndipo Iye adzasendeza kwa inu. Sambani mʼmanja mwanu, inu anthu ochimwa. Yeretsani mitima yanu, inu anthu okayikira. Chitani chisoni chifukwa cha zimene mwachita, lirani misozi. Kuseka kwanu kusanduke kulira, ndipo chimwemwe chanu chisanduke chisoni. Dzichepetseni pamaso pa Ambuye ndipo Iye adzakukwezani.
Abale musamanenane. Aliyense wonenera zoyipa mʼbale wake kapena kumuweruza, akusinjirira ndi kuweruza Malamulo. Pamene muweruza malamulo, ndiye kuti simukusunga malamulowo, koma mukuwaweruza. Pali mmodzi yekha Wopereka Malamulo ndi Woweruza. Ndiye amene akhoza kupulumutsa ndi kuwononga. Kodi ndiwe yani kuti uziweruza mnzako?
Kunyadira za Mawa
Tsono tamverani, inu amene mumati, “Lero kapena mawa tipita ku mzinda wakutiwakuti, tikatha chaka chimodzi tikuchita malonda ndi kupanga ndalama.” Chifukwa chiyani mukutero? Inu simukudziwa zimene ziti zichitike mawa. Kodi moyo wanu ndi wotani? Inu muli ngati nkhungu imene imangooneka kwa kanthawi kochepa ndipo kenaka ndikuzimirira. Koma inuyo muyenera kunena kuti, “Ambuye akalola, tikadzakhala ndi moyo, tidzachita zakutizakuti.” Koma mmene zililimu mumangodzitama ndi kudzikuza. Kudzitama konse kotereku ndi koyipa. Aliyense amene amadziwa zabwino zimene amayenera kuchita koma osazichita, ndiye kuti wachimwa.
Chenjezo kwa Achuma Opondereza Anzawo
Tsono tamverani, inu anthu achuma, lirani ndi kufuwula chifukwa cha zovuta zimene zidzakugwereni. Chuma chanu chawola ndipo njenjete zadya zovala zanu. Golide ndi siliva wanu zachita dzimbiri. Dzimbirilo lidzakhala umboni wokutsutsani ndi kuwononga mnofu wanu ngati moto. Mwadziwunjikira chuma pa masiku ano otsiriza. Taonani, ndalama za malipiro zimene munakanika kulipira aganyu aja ankasenga mʼmunda mwanu zikulira mokutsutsani. Kulira kwa okololawo kwamveka mʼmakutu mwa Ambuye Wamphamvuzonse. Mwakhala pa dziko lapansi pano moyo ofewa ndipo mwalidyera dziko lapansi. Mwadzinenepetsa pa tsiku lokaphedwa. Mwaweruza kuti ndi wolakwa ndipo mwapha munthu wosalakwa, amene sakutsutsana nanu.
Kupirira Mʼmasautso
Tsono abale, pirirani mpaka kubwera kwa Ambuye. Onani mmene amachitira mlimi. Amadikirira kuti zipatso zabwino zioneke mʼmunda mwake. Amayembekezera mokhazikika mtima kuyambira nthawi ya mvula yoyamba mpaka yotsiriza. Inunso mukhale owugwira mtima ndi osasinthika chifukwa Ambuye ali pafupi kubwera. Abale, musamanenezane zoyipa kuopa kuti mungadzaweruzidwe. Woweruza ali pa khomo!
Abale, tengerani chitsanzo cha aneneri amene anayankhula mʼdzina la Ambuye. Iwowo anakumana ndi zovuta koma anapirira. Monga mukudziwa, tinawatenga ngati odalitsika anthu amene anapirira. Munamva za kupirira kwa Yobu ndipo mwaona zimene Ambuye anamuchitira potsiriza pake. Ambuye ndi wodzaza ndi chisoni ndi chifundo.
Koposa zonse, abale anga, musamalumbire. Polumbira osamatchula kumwamba kapena dziko lapansi, kapena china chilichonse. “Inde” wanu azikhala “Inde,” ndipo “Ayi” wanu azikhala “Ayi,” kuopa kuti mungadzapezeke olakwa.
Pemphero la Chikhulupiriro
Kodi alipo wina mwa inu amene ali pa mavuto? Apemphere. Kodi wina wakondwa? Ayimbe nyimbo zolemekeza. Kodi alipo wina mwa inu akudwala? Ayitane akulu ampingo kuti adzamupempherere ndi kumudzoza mafuta mʼdzina la Ambuye. Ndipo pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa munthu wodwalayo ndipo Ambuye adzamuutsa. Ngati wachimwa adzakhululukidwa. Choncho, ululiranani machimo anu ndi kupemphererana wina ndi mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama ndi lamphamvu ndipo limagwira ntchito.
Eliya anali munthu ngati ife. Iye anapemphera mwamphamvu kuti mvula isagwe ndipo sinagwedi kwa zaka zitatu ndi theka. Kenaka anapempheranso, ndipo kumwamba kunagwetsa mvula, ndipo dziko lapansi linatulutsa zomera zake. Abale anga, ngati mmodzi wa inu apatuka pa choonadi ndipo wina wake ndi kumubweza, kumbukirani izi: Aliyense wobweza wochimwa kuchoka ku cholakwa chake, adzamupulumutsa ku imfa ndi kukwirira machimo ambiri.