- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
YESAYA
Yesaya
Yesaya
Yes
Yesaya
Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
Anthu Owukira
Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi!
Pakuti Yehova wanena kuti,
“Ndinabala ana ndi kuwalera,
koma anawo andiwukira Ine.
Ngʼombe imadziwa mwini wake,
bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake,
koma Israeli sadziwa,
anthu anga samvetsa konse.”
Haa, mtundu wochimwa,
anthu olemedwa ndi machimo,
obadwa kwa anthu ochita zoyipa,
ana odzipereka ku zoyipa!
Iwo asiya Yehova;
anyoza Woyerayo wa Israeli
ndipo afulatira Iyeyo.
Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe?
Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira?
Mutu wanu wonse uli ndi mabala,
mtima wanu wonse wafowokeratu.
Kuchokera ku phazi mpaka ku mutu
palibe pabwino,
paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda,
mabala ali magazi chuchuchu,
mabala ake ngosatsuka, ngosamanga
ndiponso ngosapaka mafuta ofewetsa.
Dziko lanu lasanduka bwinja,
mizinda yanu yatenthedwa ndi moto;
minda yanu ikukololedwa ndi alendo
inu muli pomwepo,
dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo.
Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekha
ngati nsanja mʼmunda wampesa,
ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka,
ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo.
Yehova Wamphamvuzonse akanapanda
kutisiyira opulumuka,
tikanawonongeka ngati Sodomu,
tikanakhala ngati anthu a ku Gomora.
Imvani mawu a Yehova,
inu olamulira Sodomu;
mverani lamulo la Mulungu wathu,
inu anthu a ku Gomora!
Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani
nsembe zanu zochuluka?”
“Zandikola nsembe zanu zopsereza
za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;
sindikusangalatsidwanso
ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
Ndani anakulamulirani kuti
mubwere nazo pamaso panga?
Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!
Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.
Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,
kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika
ndimadana nazo.
Zasanduka katundu wondilemera;
ndatopa kuzinyamula.
Mukamatambasula manja anu popemphera,
Ine sindidzakuyangʼanani;
ngakhale muchulukitse mapemphero anu,
sindidzakumverani.
Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
sambani, dziyeretseni.
Chotsani pamaso panu
ntchito zanu zoyipa!
Lekani kuchita zoyipa,
phunzirani kuchita zabwino!
Funafunani chilungamo,
thandizani oponderezedwa.
Tetezani ana amasiye,
muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”
Yehova akuti,
“Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.
Ngakhale machimo anu ali ofiira,
adzayera ngati thonje.
Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,
adzayera ngati ubweya wankhosa.
Ngati muli okonzeka kundimvera
mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
koma mukakana ndi kuwukira
mudzaphedwa ndi lupanga.”
Pakuti Yehova wayankhula.
Taonani momwe mzinda wokhulupirika
wasandukira wadama!
Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama;
mu mzindamo munali chilungamo,
koma tsopano muli anthu opha anzawo!
Siliva wako wasanduka wachabechabe,
vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi.
Atsogoleri ako ndi owukira,
anthu ogwirizana ndi mbala;
onse amakonda ziphuphu
ndipo amathamangira mphatso.
Iwo sateteza ana amasiye;
ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye.
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu,
Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti,
“Haa, odana nane ndidzawatha,
ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga.
Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe;
ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa,
monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala.
Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana,
aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja.
Kenaka iweyo udzatchedwa
mzinda wolungama,
mzinda wokhulupirika.”
Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama,
anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo.
Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi,
ndipo amene asiya Yehova adzatheratu.
“Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thundu
imene inkakusangalatsani;
mudzagwetsa nkhope chifukwa cha minda
imene munayipatula.
Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota,
mudzakhala ngati munda wopanda madzi.
Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma,
ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali;
motero zonse zidzayakira limodzi,
popanda woti azimitse motowo.”
Phiri la Yehova
Nazi zinthu zokhudza Yuda ndi Yerusalemu, zimene Yesaya mwana wa Amozi anaziona mʼmasomphenya:
Mʼmasiku otsiriza,
phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa
kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse,
lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,
ndipo mayiko onse adzathamangira kumeneko.
Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti,
“Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova,
ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.
Iye adzatiphunzitsa njira zake,
ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”
Malangizo adzachokera ku Ziyoni,
mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
Iye adzaweruza pakati pa mayiko,
ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri.
Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu
ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.
Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,
kapena kuphunziranso za nkhondo.
Inu nyumba ya Yakobo, bwerani,
tiyeni tiyende mʼkuwala kwa Yehova.
Tsiku la Yehova
Inu Yehova mwawakana anthu anu,
nyumba ya Yakobo.
Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa;
amawombeza mawula ngati Afilisti,
ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
Dziko lawo ndi lodzaza ndi siliva ndi golide;
ndipo chuma chawo ndi chosatha.
Dziko lawo ndi lodzaza ndi akavalo;
ndipo magaleta awo ankhondo ngosawerengeka.
Dziko lawo ndi lodzaza ndi mafano;
iwo amapembedza ntchito ya manja awo,
amagwadira zomwe anapanga ndi zala zawo.
Tsono munthu aliyense adzachepetsedwa
ndi kutsitsidwa.
Inu Yehova musawakhululukire.
Lowani mʼmatanthwe,
bisalani mʼmaenje,
kuthawa kuopsa kwa Yehova
ndi ulemerero wa ufumu wake!
Kudzikuza kwa anthu kudzatha,
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa;
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu pa tsiku limenelo.
Yehova Wamphamvuzonse wakonzeratu tsiku
limene adzatsitse onse onyada ndi odzitama,
ndipo adzagonjetsa
onse amphamvu,
tsiku la mikungudza yonse ya ku Lebanoni, yayitali ndi yoonekera patali,
ndiponso la mitengo yonse ya thundu ya ku Basani,
tsiku la mapiri onse ataliatali
ndiponso la zitunda zonse zazitali,
tsiku la nsanja zonse zazitali
ndiponso malinga onse olimba,
tsiku la sitima zapamadzi zonse za ku Tarisisi
ndiponso la mabwato onse okongola.
Kudzikuza kwa munthu kudzatha
ndipo kudzitama kwa anthu kudzawonongedwa,
Yehova yekha ndiye adzapatsidwe ulemu tsiku limenelo,
ndipo mafano onse adzatheratu.
Anthu adzathawira mʼmapanga a matanthwe
ndi mʼmaenje a nthaka,
kuthawa mkwiyo wa Yehova,
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
Tsiku limenelo anthu adzatayira
mfuko ndi mileme
mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide,
amene anawapanga kuti aziwapembedza.
Adzathawira mʼmapanga a matanthwe
ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka
kuthawa mkwiyo wa Yehova
ndiponso ulemerero wa ufumu wake,
pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
Lekani kudalira munthu,
amene moyo wake sukhalira kutha.
Iye angathandize bwanji wina aliyense?
Chiweruzo pa Yerusalemu ndi Yuda
Taonani tsopano, Ambuye
Yehova Wamphamvuzonse,
ali pafupi kuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda
zinthu pamodzi ndi thandizo;
adzachotsa chakudya chonse ndi madzi onse,
anthu amphamvu ndi asilikali ankhondo,
oweruza ndi aneneri,
anthu olosera ndi akuluakulu,
atsogoleri a ankhondo makumi asanu ndi anthu olemekezeka,
aphungu ndi anthu amatsenga ndi akatswiri pa za kulosera.
Ndidzawayikira anyamata kuti akhale mafumu awo;
ana akhanda ndiwo adzawalamulire.
Anthu adzazunzana,
munthu ndi munthu mnzake, mnansi ndi mnansi wake.
Anthu wamba adzanyoza
akuluakulu.
Munthu adzagwira mʼbale wake
mʼnyumba ya abambo awo, ndipo adzati,
“Iwe uli nawo mwinjiro, ndiye ukhale mtsogoleri wathu;
lamulira malo opasuka ano!”
Koma tsiku limenelo mʼbale wakeyo adzafuwula kuti,
“Ayi, mavuto oterewa ndilibe mankhwala ake.
Ndilibe chakudya kapena chovala mʼnyumba mwanga;
musasankhe ine kukhala mtsogoleri wa anthu.”
Yerusalemu akudzandira,
Yuda akugwa;
zokamba zawo ndi ntchito zawo nʼzotsutsana ndi Yehova,
sakulabadira ulemerero wa Mulungu.
Maonekedwe a nkhope zawo amawatsutsa;
amaonetsera poyera tchimo lawo ngati Sodomu;
salibisa tchimo lawolo.
Tsoka kwa iwo
odziputira okha mavuto.
Nena kwa olungama kuti zonse zidzawayendera bwino,
pakuti adzakondwera ndi phindu la ntchito zawo.
Tsoka kwa anthu oyipa! Mavuto ali pa iwo!
Adzalandira malipiro a zimene manja awo anachita.
Achinyamata akupondereza anthu anga,
ndipo amene akuwalamulira ndi akazi.
Aa, anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani;
akukuchotsani pa njira yanu.
Yehova wakhala pamalo pake mʼbwalo la milandu;
wakonzeka kuti aweruze anthu ake.
Yehova akuwazenga milandu
akuluakulu ndi atsogoleri a anthu ake:
“Ndinu amene mwawononga munda wanga wa mpesa;
nyumba zanu zadzaza ndi zolanda kwa amphawi.
Nʼchifukwa chiyani inu mukupsinja anthu anga,
nʼkudyera masuku pamutu amphawi?”
Akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
Yehova akunena kuti,
“Akazi a ku Ziyoni ngodzikuza kwambiri,
akuyenda atakweza makosi awo,
akukopa amuna ndi maso awo
akuyenda monyangʼama
akuliza zigwinjiri za mʼmiyendo yawo
Nʼchifukwa chake Ambuye, adzatulutsa zipere pa mitu ya akazi a ku Ziyoniwo;
Yehova adzachititsa dazi mitu yawo.”
Tsiku limenelo Ambuye adzawachotsera zodzikongoletsera zawo: za mʼmiyendo, za ku mutu za mʼkhosi, ndolo ndi zibangiri, nsalu zophimba pa nkhope, maduku, zigwinjiri za mʼmiyendo ndi malamba, mabotolo a zonunkhira ndi zithumwa, mphete ndi zipini, zovala za pa mphwando, zipewa ndi mwinjiro, zikwama, magalasi oyangʼanira, zovala zosalala, nduwira ndiponso nsalu za mʼmapewa.
Mʼmalo mwa kununkhira azidzanunkha,
mʼmalo mwa lamba, adzavala chingwe;
mʼmalo mwa tsitsi lopesa bwino, adzakhala ndi dazi;
mʼmalo mwa zovala zabwino, adzavala chiguduli;
mʼmalo mwa kunyadira kukongola adzachita manyazi.
Iwe Yerusalemu anthu ako aamuna adzaphedwa ndi lupanga,
asilikali ako adzafera ku nkhondo.
Pa zipata za Ziyoni padzakhala kubuma ndi kulira;
Iweyo udzasakazidwa nʼkukhala pansi, ukugubuduzika pa fumbi.
Tsiku limenelo akazi asanu ndi awiri
adzagwira mwamuna mmodzi,
nʼkunena kuti, “Ife tizidya chakudya chathuchathu,
ndi kuvala zovala zathu;
inu mungotilola kuti tidziyitanidwa ndi dzina lanu.
Tichotseni manyazi aumbeta!”
Nthambi ya Yehova
Tsiku limenelo Nthambi ya Yehova idzakhala yokongola ndi yaulemerero, ndipo chipatso cha mʼdziko chidzakhala chonyaditsa ndi chopereka ulemerero kwa onse opulumuka mu Israeli. Iwo amene adzatsale mu Ziyoni, amene adzatsalire mu Yerusalemu, adzatchedwa oyera, onse amene mayina awo alembedwa pakati pa anthu amoyo okhala mu Yerusalemu. Ambuye adzasambitsa akazi a Ziyoni ndi kuchotsa zonyansa zawo. Adzatsuka magazi amene anakhetsedwa mu Yerusalemu ndi mzimu wachiweruzo ndiponso mzimu wamoto. Tsono Yehova adzayika mtambo wake pamwamba ponse pa phiri la Ziyoni, ndipo pa onse amene asonkhana masana padzakhala mtambo wa utsi ndipo usiku padzakhala malawi amoto. Pamwamba pa zonse padzakhala ulemerero wa Yehova. Ulemerero wake udzakhala mthunzi wothawiramo kutentha kwa masana, udzakhala malo opeweramo mphepo ndi owusiramo mvula.
Nyimbo ya Munda Wamphesa
Ndidzamuyimbira bwenzi langa
nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:
Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa
pa phiri la nthaka yachonde.
Anatipula nachotsa miyala yonse
ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.
Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo
ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.
Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,
koma ayi, unabala mphesa zosadya.
“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,
weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa
kupambana chomwe ndawuchitira kale?
Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,
bwanji unabala mphesa zosadya?
Tsopano ndikuwuzani
chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:
ndidzachotsa mpanda wake,
ndipo mundawo udzawonongeka;
ndidzagwetsa khoma lake,
ndipo nyama zidzapondapondamo.
Ndidzawusandutsa tsala,
udzakhala wosatengulira ndi wosalimira
ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.
Ndidzalamula mitambo
kuti isagwetse mvula pa mundapo.”
Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse
ndi Aisraeli,
ndipo anthu a ku Yuda ndiwo
minda yake yomukondweretsa.
Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;
mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.
Tsoka ndi Chiweruzo
Tsoka kwa inu amene mumangokhalira kulumikiza nyumba,
ndipo mumangokhalira kuwonjezera minda,
mpaka mutalanda malo onse
kuti muzikhalamo nokha mʼdzikomo.
Yehova Wamphamvuzonse wayankhula ine ndikumva kuti,
“Ndithudi nyumba zambirizo zidzasanduka mabwinja,
nyumba zazikulu zokongolazo zidzakhala zopanda anthu.
Munda wamphesa wa maekala khumi udzatulutsa vinyo wodzaza mbiya imodzi,
kufesa madengu khumi a mbewu, zokolola zake zidzangodzaza dengu limodzi.”
Tsoka kwa iwo amene amadzuka mmamawa
nathamangira chakumwa choledzeretsa,
amene amamwa mpaka usiku
kufikira ataledzera kotheratu.
Pa maphwando awo pamakhala azeze, apangwe,
matambolini, zitoliro ndi vinyo,
ndipo sasamala ntchito za Yehova,
salemekeza ntchito za manja ake.
Motero anthu anga adzatengedwa ukapolo
chifukwa cha kusamvetsa zinthu;
atsogoleri awo olemekezeka adzafa ndi njala,
ndipo anthu wamba ochuluka adzafa ndi ludzu.
Nʼchifukwa chake ku manda sikukhuta
ndipo kwayasama kwambiri kukamwa kwake;
mʼmandamo mudzagweranso anthu otchuka a mu Yerusalemu pamodzi ndi anthu wamba ochuluka;
adzagweramo ali wowowo, nʼkuledzera kwawoko.
Ndipo munthu aliyense adzatsitsidwa,
anthu onse adzachepetsedwa,
anthu odzikuza adzachita manyazi.
Koma Yehova Wamphamvuzonse adzalemekezedwa chifukwa cha chiweruzo chake cholungama.
Ndipo Mulungu woyera adzadzionetsa kuti ndi woyera pochita chilungamo chake.
Tsono nkhosa zidzadya pamenepo ngati pabusa pawo;
ana ankhosa adzadya mʼmabwinja a anthu olemera.
Tsoka kwa amene amadzikokera tchimo ndi zingwe zachinyengo,
ndipo amadzikokera zoyipa ndi zingwe zokokera ngolo,
amene amanena kuti, “Yehova afulumire,
agwire ntchito yake mwamsanga
kuti ntchitoyo tiyione.
Ntchito zionekere,
zimene Woyerayo wa Israeli akufuna kuchita,
zichitike kuti tizione.”
Tsoka kwa amene zoyipa amaziyesa zabwino
ndipo zabwino amaziyesa zoyipa,
amene mdima amawuyesa kuwala
ndipo kuwala amakuyesa mdima,
amene zowawasa amaziyesa zotsekemera
ndipo zotsekemera amaziyesa zowawasa.
Tsoka kwa amene amadziona ngati anzeru
ndipo amadziyesa ochenjera.
Tsoka kwa zidakwa zimene zimayika mtima pa vinyo
ndipo ndi akatswiri posakaniza zakumwa,
amene amamasula olakwa chifukwa cha chiphuphu
koma amayipitsa mlandu wa munthu wosalakwa.
Nʼchifukwa chake monga momwe moto umawonongera chiputu
ndipo monga momwe udzu wowuma umapsera mʼmalawi a moto,
momwemonso mizu yawo idzawola
ndipo maluwa awo adzafota ndi kuwuluka ngati fumbi;
chifukwa akana malamulo a Yehova Wamphamvuzonse,
ndipo anyoza mawu a Woyerayo wa Israeli.
Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake;
watambasula dzanja lake pa anthuwo ndipo akuwakantha
Mapiri akugwedezeka,
ndipo mitembo ya anthu yangoti mbwee mʼmisewu ngati zinyalala.
Komabe ngakhale watero, mkwiyo wake sunaleke,
dzanja lake likanali chitambasulire;
Yehova wakweza mbendera kuyitana mtundu wa anthu akutali,
akuyitana anthuwo ndi likhweru kuti abwere kuchokera ku mathero a dziko lapansi.
Awo akubwera,
akubweradi mofulumira kwambiri!
Palibe ndi mmodzi yemwe amene akutopa kapena kupunthwa,
palibe amene akusinza kapena kugona;
palibe lamba wa mʼchiwuno amene akumasuka,
palibe chingwe cha nsapato chimene chaduka.
Mivi yawo ndi yakuthwa,
mauta awo onse ndi okoka,
ziboda za akavalo awo nʼzolimba ngati mwala wansagalabwi,
magaleta awo ndi aliwiro ngati kamvuluvulu.
Kufuwula kwawo kuli ngati kubangula kwa mkango,
amabangula ngati misona ya mkango;
imadzuma pamene ikugwira nyama
ndipo imapita nayo popanda ndi mmodzi yemwe woyipulumutsa.
Tsiku limenelo mitundu ya anthu idzabangula
ngati mkokomo wa madzi a mʼnyanja.
Ndipo wina akakayangʼana dzikolo
adzangoona mdima ndi zovuta;
ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.
Masomphenya a Yesaya
Chaka chimene mfumu Uziya anamwalira, ndinaona Ambuye atakhala pa mpando waufumu, wautali ndi wokwezedwa, ndipo mkanjo wawo unali wautali; kotero kuti unadzaza mʼNyumba ya Yehova. Pamwamba pawo panayimirira Aserafi, aliyense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi: awiri anaphimba nkhope zawo, awiri anaphimba mapazi awo, ndipo awiri ankawulukira. Ndipo Aserafiwo amafuwulirana kuti
“Woyera, woyera, woyera Yehova Wamphamvuzonse.
Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
Chifukwa cha kufuwulako maziko a zitseko ndi ziwundo anagwedezeka ndipo mʼNyumba ya Yehova munadzaza utsi.
Tsono ine ndinafuwula kuti, “Tsoka langa ine! Ndatayika! Pakuti ndine munthu wapakamwa poyipa, ndipo ndimakhala pakati pa anthu a pakamwa poyipa, ndipo ndi maso anga ndaona mfumu Yehova Wamphamvuzonse.”
Pomwepo mmodzi mwa Aserafi aja anawulukira kwa ine ali ndi khala lamoto mʼdzanja lake, khala limene analichotsa ndi mbaniro pa guwa lansembe. Ndipo anandikhudza pakamwa panga ndi khala lamotolo nati, “Taona ndakhudza pa milomo yako ndi khalali; kulakwa kwako kwachotsedwa, machimo ako akhululukidwa.”
Kenaka ndinamva mawu a Ambuye akuti, “Kodi ndidzatuma yani? Ndipo ndani adzapite mʼmalo mwathu?”
Ndipo ine ndinati, “Ndilipo. Tumeni!”
Yehova anati, “Pita ndipo ukawawuze anthu awa:
“ ‘Kumva muzimva, koma osamvetsetsa;
kupenya muzipenya koma osaona kanthu.’
Tsono anthu amenewa uwaphe mtima;
uwagonthetse makutu,
ndipo uwatseke mʼmaso.
Mwina angaone ndi maso awo,
angamve ndi makutu awo,
angamvetse ndi mitima yawo,
kenaka ndi kutembenuka mtima ndi kuchiritsidwa.”
Pamenepo ine ndinati, “Zimenezo ndi mpaka liti Inu Ambuye?”
Ndipo Iyeyo anandiyankha kuti,
“Mpaka mizinda itasanduka mabwinja
nʼkusowa wokhalamo,
mpaka nyumba zitasowa anthu okhalamo,
mpaka dziko litasanduka chipululu ndithu,
mpaka Yehova atasamutsira aliyense kutali,
dziko nʼkusiyidwa kwathunthu.
Ndipo ngakhale chigawo chakhumi cha anthu chitatsala mʼdziko,
nachonso chidzawonongedwa.
Koma monga momwe mitengo ya muwanga ndi thundu
imasiyira chitsa pamene ayidula,
chonchonso mbewu yoyera idzatsalira ngati chitsa chotsala mʼdziko.”
Yesaya Achenjeza Ahazi
Pamene Ahazi mwana wa Yotamu, mdzukulu wa Uziya anali mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka mwana wa Remaliya, mfumu ya Israeli anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu, koma sanathe kuwugonjetsa.
Tsono nyumba ya Davide inawuzidwa kuti, “Dziko la Siriya lagwirizana ndi Efereimu.” Choncho mfumu Ahazi ndi anthu ake ananjenjemera, monga momwe mitengo ya mʼnkhalango imagwedezekera ndi mphepo.
Pamenepo Yehova anawuza Yesaya kuti, “Tuluka, iwe ndi mwana wako Seariyasubu, mupite mukakumane ndi Ahazi kumapeto kwa ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu wopita ku Munda wa mmisiri wochapa nsalu. Ukamuwuze kuti, ‘Chenjera, khala phee ndipo usaope. Usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwiri zomwe zikufuka, chifukwa cha ukali woopsa wa Rezini ndi Siriya, ndiponso wa Peka mwana wa Remaliya. Mfumu ya Siriya, Efereimu ndi mwana wa Remaliya apangana kuti akuchitire choyipa. Akunena kuti, ‘Tiyeni tikalimbane ndi Yuda. Tiyeni tiliwononge ndi kuligawa; tiligawane pakati pathu, ndipo tilonge ufumu mwana wa Tabeeli kumeneko.’ Komabe zimene akunena Ambuye Yehova ndi izi:
“ ‘Zimenezo sizidzatheka,
sizidzachitika konse,
pakuti Siriya amadalira Damasiko,
ndipo Damasiko amadalira mfumu Rezini basi.
Zisanathe zaka 65
Efereimu adzawonongedwa kotheratu, sadzakhalanso mtundu wa anthu.
Dziko la Efereimu limadalira Samariya
ndipo Samariya amadalira mwana wa Remaliya basi.
Mukapanda kulimbika pa chikhulupiriro chanu,
ndithu simudzalimba konse.’ ”
Yehova anayankhulanso ndi Ahazi, “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”
Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.”
Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga? Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli. Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino. Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja. Yehova adzabweretsa pa inu, pa anthu anu ndiponso pa nyumba ya bambo wanu masiku a mavuto woti sanakhalepo kuyambira tsiku limene Efereimu anapatukana ndi Yuda. Yehova adzabweretsa mfumu ya ku Asiriya.”
Tsiku limenelo Yehova adzalizira likhweru ntchentche zochokera ku mitsinje yakutali ku Igupto, ndiponso njuchi zochokera ku dziko la Asiriya. Onsewo adzafika ndi kudzakhazikika mu zigwa zozama, mʼmingʼalu ya matanthwe ndi mʼzitsamba zonse zaminga ndiponso ponse pamene pali malo omwetsera ziweto. Tsiku limenelo Ambuye adzalemba ganyu ometa ochokera kutsidya kwa Mtsinje, ndiye mfumu ya ku Asiriya, kudzameta tsitsi lanu la ku mutu ndi la mʼmiyendo ndi ndevu zomwe. Tsiku limenelo adzangosunga ngʼombe yayikazi yayingʼono ndi mbuzi ziwiri. Ndipo chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka umene ziwetozi zidzapereka, munthuyo azidzadya chambiko. Aliyense amene adzatsalire mʼdzikomo azidzadya chambiko ndi uchi. Tsiku limenelo, paliponse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000 ndipo mtengo wake ndi wokwana masekeli asiliva 1,000, padzamera mkandankhuku ndi minga. Anthu adzapita kumeneko kukachita uzimba ali ndi uta ndi mivi, popeza kuti mʼdziko monsemo mudzakhala mkandankhuku ndi minga. Ndipo mʼmapiri monse mʼmene kale munkalimidwa ndi khasu, simudzapitamo kuopa mkandankhuku ndi minga; malowo adzasanduka odyetserako ngʼombe ndi nkhosa.
Asiriya, Chida cha Yehova
Yehova anati kwa ine, “Tenga cholembapo chachikulu ndipo ulembepo malemba odziwika bwino: Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira. Ndipo ndidzayitana wansembe Uriya ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya kuti akhale mboni zanga zodalirika.”
Ndipo ine ndinapita kwa mneneri wamkazi, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Ndipo Yehova anati kwa ine, “Umutche dzina lakuti, ‘Kusakaza-Kwamsanga Kufunkha-Kofulumira.’ Mwanayo asanayambe kudziwa kuyitana kuti, ‘Ababa’ kapena ‘Amama’ chuma cha Damasiko ndi zofunkha za Samariya zidzatengedwa ndi mfumu ya ku Asiriya.”
Yehova anayankhulanso ndi Ine;
“Popeza anthu a dziko ili akana
madzi anga oyenda mwachifatse a ku Siloamu,
ndipo akukondwerera Rezini
ndi mwana wa Remaliya,
nʼchifukwa chake Ambuye ali pafupi kubweretsa
madzi amkokomo a mtsinje wa Yufurate kudzalimbana nawo;
mfumu ya ku Asiriya ndi gulu lake lonse lankhondo.
Madziwo adzasefukira mʼngalande zake zonse
ndi mʼmagombe ake onse.
Ndipo adzalowa mwamphamvu mʼdziko la Yuda, adzasefukira,
adzapitirira mpaka kumuyesa mʼkhosi.
Mapiko ake otambasuka adzaphimba dziko lako lonse,
iwe Imanueli!”
Chitani phokoso lankhondo, inu mitundu ya anthu, ndipo munjenjemere!
Tamverani, inu mayiko onse akutali.
Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
Konzekerani nkhondo ndipo munjenjemere!
Konzani kachitidwe kanu kankhondo, koma simudzaphula kanthu,
kambiranani zochita, koma zidzalephereka,
pakuti Mulungu ali nafe.
Yehova Achenjeza Mneneri
Yehova anandiyankhula ine mwamphamvu, ndipo anandichenjeza kuti ndisamayende mʼnjira za anthuwa. Iye anati:
“Usamanene kuti ndi chiwembu,
chilichonse chimene anthuwa amati ndi chiwembu
usamaope zimene anthuwa amaziopa,
ndipo usamachite nazo mantha.
Yehova Wamphamvuzonse ndiye amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,
ndiye amene uyenera kumuopa,
ndiye amene uyenera kuchita naye mantha,
ndipo ndiye amene adzakhala malo opatulika;
koma kwa anthu a ku Yuda ndi kwa anthu a ku Israeli adzakhala
mwala wopunthwitsa,
mwala umene umapunthwitsa anthu,
thanthwe limene limagwetsa anthu.
Ndipo kwa anthu a mu Yerusalemu adzakhala ngati msampha ndi khwekhwe.
Anthu ambiri adzapunthwapo
adzagwa ndi kuthyokathyoka,
adzakodwa ndi kugwidwa.”
Manga umboniwu
ndipo umate malamulowa pamaso pa ophunzira anga.
Ndidzayembekezera Yehova,
amene akubisira nkhope yake nyumba ya Yakobo.
Ine ndidzakhulupirira Iyeyo.
Onani, ine ndili pano pamodzi ndi ana amene Yehova wandipatsa, ndife zizindikiro ndi zodabwitsa kwa Aisraeli zochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pa Phiri la Ziyoni.
Anthu akakuwuza kuti kafunsire kwa oyankhula ndi mizimu, amene amayankhula monongʼona ndi mongʼungʼudza, kodi anthu sayenera kukafunsira kwa Mulungu wawo? Chifukwa chiyani amafunsira kwa anthu akufa mʼmalo mwa kwa anthu amoyo, kuti akalandireko mawu enieni ndi malangizo? Ngati anthuwo sayankhula monga mwa mawu awa, mwa iwo mulibe kuwala. Anthu adzayendayenda mʼdziko movutika kwambiri ali ndi njala; pamene afowokeratu ndi njala, iwo adzakwiya kwambiri ndipo adzayangʼana kumwamba ndi kutemberera mfumu yawo ndi Mulungu wawo. Ndipo akadzayangʼana pa dziko lapansi adzangoona mavuto okhaokha ndi mdima woopsa ndi wodetsa nkhawa, ndipo adzaponyedwa mu mdima wandiweyani.
Ufumu wa Mesiya
Anthu amene anali ndi nkhawa, sadzakhalanso otaya mtima. Masiku amakedzana Mulungu ananyozetsa dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali, koma kutsogolo kuno dera lonse la Galileya, limene lili dziko la anthu a mitundu ina, kuyambira ku nyanja yayikulu, mʼmbali mwa Yorodani, adzalisandutsa laulemu.
Anthu oyenda mu mdima
awona kuwala kwakukulu;
kwa iwo okhala mʼdziko la mdima wandiweyani
kuwunika kwawafikira.
Inu mwauchulukitsa mtundu wanu
ndipo mwawonjezera chimwemwe chawo.
Iwo akukondwa pamaso panu,
ngati mmene anthu amakondwera nthawi yokolola,
ngatinso mmene anthu amakondwera
pamene akugawana zolanda ku nkhondo.
Monga munachitira pogonjetsa Amidiyani,
inu mwathyola goli
limene limawalemera,
ndodo zimene amamenyera mapewa awo,
ndiponso mikwapulo ya anthu owazunza.
Nsapato iliyonse ya munthu wankhondo,
ndiponso chovala chilichonse chodonthekera magazi
zidzatenthedwa pa moto
ngati nkhuni.
Chifukwa mwana watibadwira,
mwana wamwamuna wapatsidwa kwa ife,
ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake.
Ndipo adzamutcha dzina lake lakuti
Phungu Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu,
Atate Amuyaya, ndi Mfumu ya Mtendere.
Ulamuliro ndi mtendere wake
zidzakhala zopanda malire.
Iye adzalamulira ufumu wake ali pa
mpando waufumu wa Davide,
ndipo adzawukhazikitsa ndi kuwuchirikiza
mwa chiweruzo cholungama ndi pochita zachilungamo
kuyambira nthawi imeneyo mpaka muyaya.
Ndi mtima wake wonse, Yehova Wamphamvuzonse
watsimikiza kuchita zimenezi.
Mkwiyo wa Yehova pa Israeli
Ambuye atumiza mawu otsutsa Yakobo;
ndipo mawuwo agwera pa Israeli.
Anthu onse okhala mu
Efereimu ndi okhala mu Samariya,
adzadziwa zimenezi.
Iwo amayankhula modzikuza kuti,
“Ngakhale njerwa zagumuka,
koma ife tidzamanga ndi miyala yosema.
Mitanda ya mkuyu yagwetsedwa,
koma ife tidzayika mitanda ya mkungudza mʼmalo mwake.”
Koma Yehova wadzutsa adani kuti alimbane nawo
ndipo wawafulumiza adani awo kuti amenyane nawo.
Asiriya ochokera kummawa ndi Afilisti ochokera kumadzulo ndipo
ayasama pakamwa kuti adye a Israeli.
Komabe, mkwiyo wake sunawachokere,
mkono wake uli chitambasulire.
Koma anthu sanabwerere kwa amene anawakantha uja,
ngakhale kufunafuna Yehova Wamphamvuzonse.
Choncho Yehova adzadula mutu wa Israeli pamodzi ndi mchira womwe,
nthambi ya kanjedza ndi bango lomwe tsiku limodzi;
mutuwo ndiye akuluakulu ndi olemekezeka,
mchira ndiye aneneri ophunzitsa zabodza.
Amene amatsogolera anthuwa ndiwo amawasocheretsa,
ndipo otsogoleredwa amatayika.
Nʼchifukwa chake Ambuye adzakondwera nawo achinyamata,
ngakhale kuwachitira chifundo ana amasiye ndi akazi amasiye,
pakuti aliyense ndi wosapembedza Mulungu ndiponso ndi wochimwa ndipo
aliyense amayankhula zopusa.
Komabe, mkwiyo wake sunawachokere,
mkono wake uli chitambasulire.
Ndithu kuyipa kwa anthuwo kumayaka ngati moto;
moto wake umanyeketsa mkandankhuku ndi minga,
umayatsa nkhalango yowirira,
ndipo utsi wake umachita kuti toloo ngati mtambo.
Dziko lidzatenthedwa ndi ukali wa Yehova Wamphamvuzonse,
dziko lidzatenthedwa
ndipo anthu adzakhala ngati nkhuni zosonkhera moto;
palibe munthu amene adzachitire chifundo mʼbale wake.
Kudzanja lamanja adzapeza chakudya nʼkudya,
koma adzakhalabe ndi njala;
kudzanja lamanzere adzapeza chakudya nʼkudya,
koma sadzakhuta.
Aliyense azidzadya ana ake omwe.
Manase adzadya Efereimu ndipo Efereimu adzadya Manase;
onsewa pamodzi adzadya Yuda.
Komabe pa zonsezi, mkwiyo wake sunawachokere,
mkono wake uli chitambasulire.
Tsoka kwa anthu amene amapanga malamulo opanda chilungamo,
kwa iwo amene amalemba zongovutitsa anzawo,
kuwalanda anthu osauka ufulu wawo
ndi kumana chilungamo osautsidwa pakati pa anthu anga,
amalanda zinthu za akazi amasiye
ndi kubera ana amasiye.
Kodi mudzatani pa tsiku la chilango,
pofika chiwonongeko chochokera kutali?
Kodi mudzathawira kwa yani kuti akuthandizeni?
Nanga chuma chanu mudzachisiya kuti?
Kudzatsala nʼkungozolika mwamanyazi pakati pa anthu ogwidwa
kapena kufa pamodzi ndi ophedwa.
Komabe pa zonsezi mkwiyo wake sunawachokere,
mkono wake uli chitambasulire.
Chiweruzo cha Mulungu pa Asiriya
“Tsoka kwa mfumu ya ku Asiriya, chikwapu cha mkwiyo wanga,
iye ndiye ndodo ya mkwiyo wanga!
Ndidzamutuma kukalimbana ndi mtundu wosapembedza Mulungu,
ndidzamutumiza kukalimbana ndi anthu amene amandikwiyitsa Ine,
kukafunkha ndi kulanda chuma,
ndi kuwapondereza pansi ngati matope a mʼmisewu.
Koma izi si zimene akufuna kukachita,
izi si zimene zili mʼmaganizo mwake;
cholinga chake ndi kukawononga,
kukapulula mitundu yambiri ya anthu.
Iye akuti, ‘Kodi atsogoleri anga ankhondo si mafumu okhaokha?’
‘Kodi Kalino sanagonjetsedwe monga Karikemesi?
Kodi Hamati sali ngati Aripadi,
nanga Samariya sali ngati Damasiko?
Dzanja langa linakantha maufumu a anthu opembedza mafano,
mafumu amene mafano awo ndi aakulu kupambana Yerusalemu ndi Samariya;
nanga Ine nʼkulephera kodi kuwononga Yerusalemu pamodzi ndi mafano ake
monga ndinakanthira Samariya pamodzi ndi mafano ake?’ ”
Ambuye akadzamaliza ntchito yonse yolanga phiri la Ziyoni ndi Yerusalemu adzalanganso mfumu ya ku Asiriya chifukwa cha kudzitama ndi kunyada kwake. Pakuti mfumuyo ikuti,
“ ‘Ndachita zimenezi ndi dzanja langa,
ndiponso ndi nzeru zanga, chifukwa ndine wozindikira zinthu.
Ndinachotsa malire a mitundu ya anthu,
ndinafunkha chuma chawo;
ndinagonjetsa mafumu awo monga munthu wamphamvu.
Dzanja langa lagwira chuma cha mitundu ya anthu
ngati momwe munthu amagwirira chisa cha mbalame,
ngati momwe anthu amatolera mazira osiyidwa,
motero inenso ndinasonkhanitsa mayiko onse;
palibe mbalame imene inakupiza mapiko ake,
kapena kuyasama kukamwa kuti ilire.’ ”
Kodi nkhwangwa ingathe kudzikuza kupambana woyigwiritsa ntchito,
kapena macheka angathe kudzikuza kupambana wowagwiritsa ntchito?
Ndiye kukhala ngati kuti chikwapu chikuzunguza munthu amene wachinyamula,
kapena ngati kuti ndodo ikuopseza amene wayinyamula!
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
adzatumiza matenda owondetsa kwa ankhondo amphamvu;
kunyada kwa mfumuyo kudzapsa
ndi moto wosazima.
Mulungu, Kuwala kwa Israeli, adzakhala ngati moto,
Woyera uja wa Israeli adzakhala ngati malawi a moto.
Motowo udzawatentha ndi kuwapsereza
ngati minga ndi mkandankhuku pa tsiku limodzi.
Ankhondo ake adzawonongedwa
ngati nkhalango yayikulu
ndi ngati nthaka yachonde.
Mitengo yotsalira ya mʼnkhalango zake idzakhala yochepa kwambiri,
yoti ndi mwana yemwe ndi kuyiwerenga.
Aisraeli Otsala
Tsiku limenelo otsalira a ku Israeli,
opulumuka a nyumba ya Yakobo,
sadzadaliranso anthu
amene anawakantha,
koma adzadalira Yehova,
Woyerayo wa Israeli.
Otsalira adzabwerera, otsalira a Yakobo
adzabwerera kwa Mulungu Wamphamvu.
Iwe Israeli, ngakhale anthu ako achuluke ngati mchenga wa ku nyanja,
otsala okha ndiwo adzabwerere.
Chiwonongeko chalamulidwa,
chidzaonetsa chilungamo chosefukira.
Ambuye Yehova Wamphamvuzonse adzawononga ndithu dziko lonse
monga momwe analamulira.
Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti,
“Inu anthu anga okhala mu Ziyoni,
musawaope Asiriya,
amene amakukanthani ndi ndodo
nakumenyani ndi zibonga monga mmene Igupto anachitira.
Patsala pangʼonongʼono kuti mkwiyo wanga uchoke pa inu
ndipo ndidzaonetsa ukali wanga pa iwo mpaka kuwawononga.”
Yehova Wamphamvuzonse adzawakwapula ndi chikwapu,
monga momwe anakwapulira Amidiyani ku thanthwe la Orebu;
ndipo adzatukula ndodo yake pa madzi
ndikuwalanga monga analangira Igupto pa nyanja.
Tsiku limenelo katundu wawo adzachotsedwa pa mapewa anu,
goli lawo lidzachoka mʼkhosi mwanu;
golilo lidzathyoka
chifukwa cha kunenepa kwambiri.
Adani alowa mu Ayati
apyola ku Migironi;
asunga katundu wawo ku Mikimasi.
Adutsa pa mpata uja, ndipo akuti,
“Tikagona ku Geba”
Rama akunjenjemera;
Gibeya, mzinda wa Saulo ukuthawa.
Lilani mokweza, inu anthu a ku Galimu!
Tchera khutu, iwe Laisa!
Iwe Anatoti wosauka!
Anthu a ku Madimena akuthawa;
anthu a ku Gebimu bisalani.
Lero lomwe lino adaniwo adzayima ku Nobu;
adzagwedeza mikono yawo,
kuopseza anthu a ku Ziyoni,
pa phiri la Yerusalemu.
Taonani, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse,
adzadula mwamphamvu nthambi za mitengo,
mitengo yodzikweza idzadulidwa,
mitengo yayitali idzagwetsedwa.
Yehova adzadula ndi nkhwangwa mitengo ya mʼnkhalango yowirira;
Lebanoni adzagwa pamaso pa Wamphamvu.
Za Ufumu Wamtendere wa Mesiya
Padzatuluka mphukira pa tsinde la Yese
ndipo nthambi idzaphukira kuchokera ku mizu yake.
Mzimu wa Yehova udzakhala pa iye
Mzimu wanzeru ndi wa kumvetsa zinthu,
Mzimu wauphungu ndi wamphamvu,
Mzimu wachidziwitso ndi wakuopa Yehova.
Ndipo kuopa Yehova ndiye chidzakhale chinthu chomukondweretsa.
Iye sadzaweruza potsata zooneka pamaso,
kapena kugamula mlandu potsata zakumva;
koma amphawi adzawaweruza mwachilungamo,
adzaweruza mwachilungamo mlandu wa anthu osauka a dziko lapansi.
Iye adzakantha dziko lapansi ndi mawu ake;
atalamula Iyeyu anthu oyipa adzaphedwa.
Chilungamo chidzakhala ngati lamba wake
ndipo kukhulupirika kudzakhala ngati chomangira mʼchiwuno mwake.
Mʼmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wankhosa,
kambuku adzagona pansi pamodzi ndi mwana wambuzi,
mwana wangʼombe ndi mwana wa mkango adzadyera limodzi
ndipo mwana wamngʼono adzaziweta.
Ngʼombe yayikazi ndi chimbalangondo zidzadya pamodzi,
ana awo adzagona pamodzi,
ndipo mkango udzadya udzu ngati ngʼombe.
Mwana wakhanda adzasewera pa dzenje la mamba,
ndipo mwana wamngʼono adzapisa dzanja lake ku phanga la mphiri osalumidwa.
Sipadzakhala chilichonse chopweteka kapena chowononga
pa phiri lopatulika la Yehova,
pakuti anthu a dziko lapansi adzadzaza ndi nzeru yotha kudziwa Yehova
monga momwe nyanja imadzazira ndi madzi.
Tsiku limenelo mfumu yatsopano yochokera pa Muzu wa Yese idzakhala ngati chizindikiro kwa anthu a mitundu yonse. Mitundu ya anthu idzasonkhana kwa Iye, ndipo malo awo okhalapo adzakhala aulemerero. Tsiku limenelo Ambuye adzatambasula dzanja lake kachiwiri kuti awombole anthu ake otsalira ku Asiriya, ku Igupto, ku Patirosi, Kusi, ku Elamu, ku Sinana, ku Hamati ndi pa zilumba za nyanja yamchere.
Adzakwezera mitundu ya anthu mbendera,
ndipo adzasonkhanitsa otayika a ku Israeli;
Iye adzasonkhanitsa anthu obalalika a ku Yuda
kuchokera ku mbali zonse zinayi za dziko lapansi.
Nsanje ya Efereimu idzatha,
ndipo adani a Yuda adzatha;
Efereimu sadzachitira nsanje Yuda,
ngakhale Yuda sadzamuda Efereimu.
Yuda ndi Efereimu adzathira nkhondo pa Afilisti mbali ya kumadzulo;
ndipo onsewo pamodzi adzalanda zinthu za anthu a kummawa.
Adzalimbana ndi Edomu ndi Mowabu,
ndipo Aamoni adzawagonjera.
Yehova adzaphwetsa
mwendo wa nyanja ya Igupto;
adzatambasula dzanja lake ndipo adzawombetsa mphepo yotentha
pa mtsinje wa Yufurate.
Iye adzawugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri
kuti anthu athe kuwoloka powuma atavala nsapato.
Padzakhala msewu waukulu woti ayendepo anthu ake otsalira
amene anatsalira ku Asiriya,
monga mmene panali msewu waukulu woyendapo Israeli
pamene amachokera ku Igupto.
Nyimbo za Mayamiko
Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:
“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;
chifukwa ngakhale munandipsera mtima,
mkwiyo wanu wachoka,
ndipo mwanditonthoza.
Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.”
Mudzakondwera popeza Yehova
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
Tsiku limenelo mudzati:
“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
Kulangidwa Kwa Babuloni
Uthenga onena za Babuloni umene Yesaya mwana wa Amozi anawulandira:
Kwezani mbendera yankhondo pa phiri loti see,
muwafuwulire ankhondo;
muwakodole kuti adzalowe pa zipata
za anthu olemekezeka.
Ine Yehova, ndalamulira ankhondo anga;
ndasonkhanitsa ankhondo anga kuti akhale zida zanga zolangira
amene amadzikuza ndi chipambano changa.
Tamvani phokoso ku mapiri,
likumveka ngati phokoso la gulu lalikulu la anthu!
Tamvani phokoso pakati pa maufumu,
ngati kuti mitundu ya anthu ikusonkhana pamodzi!
Yehova Wamphamvuzonse akukhazika asilikali ake mokonzekera
kuchita nkhondo.
Iwo akuchokera ku mayiko akutali,
kuchokera kumalekezero a dziko
Yehova ali ndi zida zake za nkhondo
kuti adzawononge dziko la Babuloni.
Lirani mofuwula, pakuti tsiku la Yehova layandikira;
lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
Zimenezi zinafowoketsa manja onse,
mtima wa munthu aliyense udzachokamo.
Anthu adzagwidwa ndi mantha aakulu,
zowawa ndi masautso zidzawagwera;
adzamva zowawa zonga amamva mayi pobereka.
Adzayangʼanana mwamantha,
nkhope zawo zikufiira ngati malawi amoto.
Taonani, tsiku la Yehova likubwera,
tsiku lopanda chisoni, lawukali ndi lamkwiyo;
kudzasandutsa dziko kuti likhale chipululu
ndi kuwononga anthu ochimwa a mʼmenemo.
Nyenyezi zakumwamba ndiponso zonse zamlengalenga
sizidzaonetsa kuwala kwawo.
Dzuwa lidzada potuluka,
ndipo mwezi sudzawala konse.
Ndidzalanga dziko lonse chifukwa cha zolakwa zake,
anthu oyipa ndidzawalanga chifukwa cha machimo awo.
Ndidzathetsa kunyada kwa odzikuza,
ndipo ndidzatsitsa kudzitukumula kwa anthu ankhanza.
Ndidzasandutsa anthu kukhala ovuta kupeza kuposa mmene amasowera golide wabwino.
Iwo sazidzapezekapezeka kuposa mmene amasowera golide wa ku Ofiri.
Tsono ndidzagwedeza miyamba
ndipo dziko lapansi lidzachoka pa maziko ake.
Izi zidzachitika chifukwa cha ukali wa Wamphamvuzonse
pa tsiku la mkwiyo wake woopsa.
Ngati mbawala zosakidwa,
ngati nkhosa zopanda wozikusa,
munthu aliyense adzabwerera kwa anthu akwawo,
aliyense adzathawira ku dziko lake.
Aliyense amene atadzapezeke ndi kugwidwa
adzaphedwa momubaya ndi lupanga.
Ana awo akhanda adzaphwanyidwa iwo akuona;
nyumba zawo zidzafunkhidwa ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
Taona, Ine ndidzadzutsa Amedi amene safuna siliva
ndipo sasangalatsidwa ndi golide,
kuti amenyane ndi Ababuloni.
Adzapha anyamata ndi mauta awo;
sadzachitira chifundo ana
ngakhale kumvera chisoni ana akhanda.
Babuloni, ufumu wake ndi waulemerero kuposa mafumu onse.
Anthu ake amawunyadira.
Koma Yehova adzawuwononga
ngati mmene anawonongera Sodomu ndi Gomora.
Anthu sadzakhalamonso
kapena kukhazikikamo pa mibado yonse;
palibe Mwarabu amene adzayimike tenti yake,
palibe mʼbusa amene adzawetamo ziweto zake.
Koma nyama zakuthengo ndizo zidzakhale kumeneko,
nyumba zake zidzadzaza ndi nkhandwe;
mu mzindamo muzidzakhala akadzidzi,
ndipo atonde akuthengo azidzalumphalumphamo.
Mu nsanja zake muzidzalira afisi,
mʼnyumba zake zokongola muzidzalira nkhandwe.
Nthawi yake yayandikira
ndipo masiku ake ali pafupi kutha.
Yehova adzachitira chifundo Yakobo;
adzasankhanso Israeli
ndi kuwalola kuti akhalenso mʼdziko lawo.
Alendo adzabwera kudzakhala nawo
ndi kudziphatika okha kukhala ngati a mʼnyumba ya Yakobo.
Anthu a mitundu ina adzaperekeza a Israeli
ku dziko lawo.
Tsono Aisraeli adzasandutsa anthu a mitundu ina aja
kukhala antchito awo aamuna ndi aakazi mʼdziko la Yehova.
Ndiye kuti Aisraeli adzasandutsa akapolo anthu amene kale anali ambuye awo.
Iwo adzasandutsa akapolo anthu amene kale ankawalamulira ndi kuwazunza.
Yehova akadzakupumitsani ku zowawa ndi mavuto, ndiponso kuntchito yakalavulagaga imene ankakugwiritsani, mudzayankhula monyogodola mfumu ya Babuloni kuti,
Wopsinja uja watha!
Ukali wake uja watha!
Yehova wathyola chikwapu cha anthu oyipa,
Iye waphwanya ndodo ya olamulira.
Mfumu ya ku Babuloni inkakantha mitundu ya anthu mwaukali
powamenya kosalekeza,
Iyo inkagonjetsa anthu a mitundu ina mwaukali
ndikuwazunza kosalekeza.
Koma tsopano mayiko onse ali pa mpumulo ndi pa mtendere;
ndipo akuyimba mokondwa.
Ngakhale mitengo ya payini ndi mikungudza ya ku Lebanoni
ikuyimba za iwe mokondwa ndipo ikuti,
“Chigwetsedwere chako pansi,
palibe wina anabwera kudzatigwetsa.”
Ku manda kwatekeseka
kuti akulandire ukamabwera;
mizimu ya anthu akufa, aja amene anali atsogoleri
a dziko lapansi, yadzutsidwa.
Onse amene anali mafumu a mitundu ya anthu
ayimiritsidwa pa mipando yawo.
Onse adzayankha;
adzanena kwa iwe kuti,
“Iwenso watheratu mphamvu ngati ife;
Iwe wafanana ndi ife.”
Ulemerero wako wonse walowa mʼmanda,
pamodzi ndi nyimbo za azeze ako;
mphutsi zayalana pogona pako
ndipo chofunda chako ndi nyongolotsi.
Wagwa pansi bwanji kuchoka kumwamba,
iwe nthanda, mwana wa mʼbandakucha!
Wagwetsedwa pansi pa dziko lapansi,
Iwe amene unagonjetsapo mitundu ya anthu!
Mu mtima mwako unkanena kuti,
“Ndidzakwera mpaka kumwamba;
ndidzakhazika mpando wanga waufumu
pamwamba pa nyenyezi za Mulungu;
ndidzakhala pa mpando waufumu pa phiri losonkhanirako,
pamwamba penipeni pa phiri la kumpoto.
Ndidzakwera pamwamba pa mitambo;
ndidzafanana ndi Wammwambamwamba.”
Koma watsitsidwa mʼmanda
pansi penipeni pa dzenje.
Anthu akufa adzakupenyetsetsa
nadzamalingalira za iwe nʼkumati,
“Kodi uyu ndi munthu uja anagwedeza dziko lapansi
ndi kunjenjemeretsa maufumu,
munthu amene anasandutsa dziko lonse chipululu,
amene anagwetsa mizinda yake
ndipo sankalola kuti anthu ogwidwa abwerere kwawo?”
Mafumu onse a mitundu ya anthu akugona mwaulemu
aliyense mʼmanda akeake.
Koma iwe watayidwa kunja kwa manda ako,
ngati nthambi yowola ndi yonyansa.
Mtembo wako waphimbidwa ndi anthu ophedwa;
amene anabayidwa ndi lupanga,
anatsikira mʼdzenje lamiyala
ngati mtembo woponderezedwa.
Sudzayikidwa nawo mʼmanda mwaulemu,
chifukwa unawononga dziko lako
ndi kupha anthu ako.
Zidzukulu za anthu oyipa
sizidzakumbukika nʼpangʼono pomwe.
Konzani malo woti muphere ana ake aamuna
chifukwa cha machimo a makolo awo;
kuti angadzuke ndi kulanda dziko lapansi
ndi kulidzaza dziko lonselo ndi mizinda yawo.
Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Ine ndidzathira nkhondo mzinda wa Babuloni.
Ndidzachotseratu mu Babuloni dzina lake ndi onse otsaliramo.
Ndiye kuti sipadzakhala ana kapena zidzukulu,”
akutero Yehova.
“Ndidzawusandutsa mzindawo malo okhalamo anungu
ndiponso dambo lamatope;
ndidzawusesa ndi tsache lowononga,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Za Kulangidwa kwa Asiriya
Yehova Wamphamvuzonse walumbira kuti,
“Ndithudi, monga ndaganizira ndidzachitadi choncho,
ndipo monga momwe ndatsimikizira zidzakhala momwemo ndithu.
Ndidzawawononga Asiriya mʼdziko langa;
ndidzawapondereza ndi mapazi pa mapiri anga;
ndidzachotsa goli lawo pa anthu anga,
ndipo ndidzachotsa katundu wawo pa mapewa awo.”
Izi ndizo ndakonza kuti zichitike pa dziko lonse lapansi,
ndatambasula dzanja pa anthu a mitundu yonse.
Pakuti Yehova Wamphamvuzonse watsimikiza, ndipo ndani angamuletse?
Dzanja lake latambasulidwa ndipo ndani angalibweze?
Za Kulangidwa kwa Afilisti
Uthenga uwu unabwera chaka chimene mfumu Ahazi anamwalira:
Musakondwere inu Afilisti nonse
kuti Asiriya amene anali ngati ndodo yokukanthani anathedwa;
chifukwa kuchokera ku njoka yomweyi (mfumu ya Aasiriya) mudzatuluka mphiri,
ndipo chipatso chake chidzakhala njoka yaliwiro ndiponso yaululu.
Osaukitsitsa adzapeza chakudya
ndipo amphawi adzakhala mwamtendere.
Koma anthu ako ndidzawawononga ndi njala,
ndipo njalayo idzapha ngakhale opulumuka ako.
Lirani kwambiri, anthu a pa chipata! Fuwulani kwambiri, anthu a mu mzinda!
Njenjemerani ndi mantha, inu Afilisti nonse!
Mtambo wa utsi ukuchokera kumpoto,
ndipo palibe wamantha pakati pa ankhondo ake.
Kodi tidzawayankha chiyani
amithenga a ku Filisitiya?
“Yehova wakhazikitsa Ziyoni,
ndipo mu mzinda wakewu, anthu ozunzika apeza populumukira.”
Za Kulangidwa kwa Mowabu
Uthenga wonena za Mowabu:
Popeza kuti mu usiku umodzi wokha mzinda wa Ari wa ku Mowabu wawonongedwa,
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Mzinda wa Kiri wawonongedwa,
wawonongedwa pa usiku umodzi wokha.
Anthu a ku Diboni akupita ku nyumba ya milungu yawo,
akupita ku malo awo achipembedzo kukalira;
anthu a ku Mowabu akulirira mofuwula mzinda wa Nebo ndi wa Medeba.
Mutu uliwonse wametedwa mpala,
ndipo ndevu zonse zametedwa.
Mʼmisewu akuvala ziguduli;
pa madenga ndi mʼmabwalo
aliyense akulira mofuwula,
misozi ili pupupu.
Anthu a ku Hesiboni ndi Eleali akulira mofuwula,
mawu awo akumveka mpaka ku Yahazi.
Kotero asilikali a ku Mowabu akulira mofuwula,
ndipo ataya mtima.
Inenso ndikulirira Mowabu;
chifukwa othawa nkhondo ake akupita akulira ku chikweza cha Luluti mpaka ku Zowari
ndi Egilati-Selisiya
akupita akulira ku chikweza cha Luhiti,
Akulira mosweka mtima
pa njira yopita ku Horonaimu;
akulira mosweka mtima chifukwa cha chiwonongeko chawo.
Madzi a ku Nimurimu aphwa
ndipo udzu wauma;
zomera zawonongeka
ndipo palibe chomera chobiriwira chatsala.
Kotero kuti chuma chomwe anachipeza ndi kuchisunga,
achitenga kuti awoloke nacho chigwembe cha Misondozi.
Kulira kwawo kukumveka mʼdziko lonse la Mowabu;
kulira kwawo kosweka mtima kukumveka
mpaka ku Egilaimu ndi Beeri-Elimu.
Madzi a ku Dimoni afiira ndi magazi,
komabe ndidzabweretsa zina zambiri pa Dimoni,
mkango woti udzagwire aliyense othawa mu Mowabu
ndi aliyense wotsala mʼdzikomo.
Anthu a ku Mowabu
atumiza mphatso za ana ankhosa onenepa,
kuchokera ku Sela kudutsa chipululu
mpaka kukafika ku phiri la Ziyoni.
Monga momwe mbalame zimawulukira uku ndi uku
akazimwaza mʼchisa,
momwemonso akazi a ku Mowabu
akuyendayenda ku madooko a Arinoni.
Amowabu aja anawuza a ku Yuda kuti,
“Tiwuzeni chochita, gamulani zoti tichite.
Inu mutiteteze kwa adani anthu.
Mukhale ngati mthunzi wathu dzuwa lili pa liwombo.
Mutibise,
musatipereke ife othawa nkhondo kwa adani athu.
Lolani kuti anthu othawa nkhondo a ku Mowabu azikhala pakati panu;
mukhale populumukira pawo kwa wowonongayo.”
Nthawi idzafika ndipo wozunzayo sadzakhalaponso,
kuwononga kudzaleka;
waukaliyo adzachoka mʼdzikomo.
Mpando waufumu udzakhazikitsidwa mwachikondi;
mmodzi mwa zidzukulu za Davide adzakhalapo mokhulupirika.
Iyeyo poweruza adzatsata chilungamo
ndipo adzalimbikitsa kuchita zachilungamo.
Tinamva kuti Mowabu anadzikuza kwambiri.
Kunyada kwawo
ndi kunyogodola kwawo ndi kudzitama kwawo,
zonse ndi zopanda phindu.
Nʼchifukwa chake Amowabu akulira kwambiri;
iwo akulirira dziko lawo.
Akubuma momvetsa chisoni
chifukwa cha makeke a mphesa a ku Kiri Hareseti.
Minda ya ku Hesiboni yauma,
minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga.
Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda
minda ya mpesa wabwino,
imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri,
mpaka kutambalalira ku chipululu.
Mizu yake inakafika
mpaka ku tsidya la nyanja.
Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri,
chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima.
Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali,
ndikukunyowetsani ndi misozi!
Mwalephera kupeza zokolola,
chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
Chimwemwe ndi chisangalalo zalekeka ku minda yanu ya zipatso;
palibe amene akuyimba kapena kufuwula mʼminda ya mpesa;
palibe amene akupsinya vinyo ku malo opsinyira mphesa,
pakuti ndathetsa kufuwula.
Chifukwa chake moyo wanga ukulira ngati pangwe kulirira Mowabu,
mtima wanga ukubuwula chifukwa cha Kiri Hareseti.
Ngakhale anthu a ku Mowabu
apite ku malo awo achipembedzo
koma amangodzitopetsa ndi kutaya nthawi chabe
chifukwa sizidzatheka.
Awa ndi mawu amene Yehova wayankhula kale zokhudza Mowabu. Koma tsopano Yehova akuti, “Zisanathe zaka zitatu, potsata mʼmene munthu waganyu amawerengera, ulemerero wa Mowabu udzakhala utatheratu ndipo anthu ake ambiri adzakhala atawonongeka, ndipo opulumuka ake adzakhala ochepa ndi ofowoka.”
Uthenga Wotsutsa Damasiko
Uthenga wonena za Damasiko:
“Taonani, mzinda wa Damasiko sudzakhalanso mzinda,
koma udzasanduka bwinja.
Mizinda ya Aroeri idzakhala yopanda anthu
ndipo idzakhala ya ziweto, zimene zidzagona pansi
popanda wina woziopseza.
Ku Efereimu sikudzakhalanso linga,
ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu;
Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu
monga anthu a ku Israeli,”
akutero Yehova Wamphamvuzonse.
“Tsiku limenelo ulemerero wa Yakobo udzazimirira;
ndipo chuma chake chidzasanduka umphawi.
Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu
umene anatsiriza kukolola.
Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu
anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale
monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni
kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi
mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,”
akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
Tsiku limenelo anthu adzayangʼana Mlengi wawo
ndipo adzatembenukira kwa Woyerayo wa Israeli.
Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe,
ntchito ya manja awo,
ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera,
ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu;
simunakumbukire Thanthwe, linga lanu.
Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino,
ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
nimuyembekeza kuti zikule tsiku lomwelo
ndi kuphukira maluwa mmawa mwake,
komabe zimenezi sizidzakupindulirani
pa tsiku la mavuto.
Aa, mkokomo wa anthu a mitundu yambiri,
akusokosa ngati kukokoma kwa nyanja!
Aa, phokoso la anthu a mitundu ina,
akusokosa ngati mkokomo wa madzi amphamvu!
Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri,
koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula.
Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri,
ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika,
ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa.
Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu,
gawo la amene amatibera zinthu zathu.
Za Kulangidwa kwa Kusi
Tsoka kwa anthu a ku Kusi.
Kumeneko kumamveka mkokomo wa mapiko a dzombe.
Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo,
mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi,
ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro,
kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala,
ndi woopedwa ndi anthu.
Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena.
Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
Inu nonse anthu a pa dziko lonse,
inu amene mumakhala pa dziko lapansi,
pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri
yangʼanani,
ndipo pamene lipenga lilira
mumvere.
Pakuti Yehova akunena kwa ine kuti,
“Ndili chikhalire ku malo anga kuno, ndidzakhala chete, ndi kumangoyangʼana,
monga momwe dzuwa limawalira nthawi yotentha,
monganso momwe mame amagwera usiku pa nthawi yotentha yokolola.”
Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka
ndiponso mphesa zitayamba kupsa,
Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira,
ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama
ndiponso zirombo zakuthengo;
mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe,
ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse,
zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala,
kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe,
mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo,
anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.
Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.
Za Kulangidwa kwa Igupto
Uthenga onena za Igupto:
Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro,
ndipo akupita ku Igupto.
Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake,
ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.
“Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha;
mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake,
mnansi ndi mnansi wake,
mzinda ndi mzinda unzake,
ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
Aigupto adzataya mtima
popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo;
adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa,
kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
Ndidzawapereka Aigupto
kwa olamulira ankhanza,
ndipo mfumu yoopsa idzawalamulira,”
akutero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse.
Madzi a mu mtsinje wa Nailo adzaphwa,
ndipo mʼmbali mwa mtsinje mudzangʼaluka ndi kuwuma.
Ngalande zake zidzanunkha;
ndipo mitsinje ya Igupto idzayamba kuchepa ndi kuwuma.
Bango ndi dulu zidzafota,
ndiponso zomera za mʼmphepete mwa Nailo
ndi ku mathiriro a mtsinjewo.
Zonse zodzalidwa mʼmbali mwa Nailo
zidzawuma, zidzawuluzika ndipo sizidzaonekanso.
Asodzi adzabuwula ndi kudandaula,
onse amene amaponya mbedza mu Nailo;
onse amene amaponya makoka mʼmadzi
adzalira.
Amene amagwira ntchito yopota thonje adzataya mtima,
anthu oluka nsalu zofewa zabafuta adzataya chiyembekezo.
Akatswiri opanga nsalu adzangoti kakasi,
ndipo anthu onse ogwira ntchito yolipidwa adzatheratu mphamvu.
Akuluakulu a ku Zowani ndi zitsiru;
aphungu a nzeru a Farao amalangiza zopusa.
Kodi mungathe kunena bwanji kwa Farao kuti,
“Ine ndine mmodzi mwa anthu anzeru,
wophunzira wa mafumu akale?”
Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti?
Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa
zimene Yehova Wamphamvuzonse
wakonza kuchitira dziko la Igupto.
Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru,
atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa;
atsogoleri a dziko la Igupto
asocheretsa anthu a dzikolo.
Yehova wasocheretsa
anthu a ku Igupto.
Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita,
ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.
Palibe chimene munthu wa mu Igupto angachite,
mtsogoleri kapena wotsatira, nthambi ya kanjedza kapena bango.
Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga. Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.
Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.
Tsiku limenelo mʼkati mwa dziko la Igupto mudzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake adzayikira Yehova mwala wachikumbutso. Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa. Kotero Yehova adzadziulula yekha kwa Aigupto, ndipo tsiku limenelo adzadziwa Yehova. Adzapembedza Yehova popereka nsembe ndi popereka zopereka zachakudya; Adzalumbira kwa Yehova ndipo adzachita zimene alumbirazo. Yehova adzakantha Aigupto ndi mliri. Iye adzawakanthadi ndipo kenaka adzawachiritsa. Aigupto adzatembenukira kwa Yehova ndipo Iye adzamva madandawulo awo ndi kuwachiritsa.
Tsiku limenelo kudzakhala msewu waukulu wochoka ku Igupto kupita ku Asiriya. Aasiriya adzapita ku Igupto ndi Aigupto ku Asiriya. Aigupto ndi Aasiriya adzapembedza pamodzi. Tsiku limenelo Israeli adzakhala pamodzi ndi Igupto ndi Asiriya, mayiko atatuwa adzakhala dalitso pa dziko lapansi. Yehova Wamphamvuzonse adzawadalitsa, ndi mawu awa, “Adalitsike anthu anga Aigupto, Aasiriya, ntchito ya manja anga, ndi Aisraeli osankhidwa anga.”
Za Chilango cha Igupto ndi Kusi
Mʼchaka chimene mkulu wankhondo wotumidwa ndi mfumu ya ku Asiriya, anabwera ku Asidodi ndi kuwuthira nkhondo ndi kuwulanda, nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.
Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi, momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto. Amene ankadalira Kusi, ndiponso amene ankadzitukumula chifukwa cha Igupto adzakhumudwa ndi kuchita manyazi. Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”
Za Chilango cha Babuloni
Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja.
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja,
kuchokera ku chipululu,
dziko lochititsa mantha.
Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya:
Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga.
Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda!
Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha,
ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka;
ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva,
ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
Mtima wanga ukugunda,
ndipo ndikunjenjemera ndi mantha;
chisisira chimene ndakhala ndikuchifuna
chasanduka chinthu choopsa kwa ine.
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo,
akuyala mphasa,
akudya komanso kumwa!
Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo,
pakani mafuta zishango zanu!”
Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi;
“Pita, kayike mlonda
kuti azinena zimene akuziona.
Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo
ndipo akuyenda awiriawiri,
okwera pa bulu
kapena okwera pa ngamira,
mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
Ndipo mlondayo anafuwula kuti,
“Ambuye anga, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa nsanja yolondera;
Usiku uliwonse ndimakhala pa malo anga olondera.
Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta
ali ndi gulu la akavalo.
Mmodzi wa iwo akuti,
‘Babuloni wagwa, wagwa!
Mafano onse a milungu yake
agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”
Inu anthu anga opunthidwa ndi kupetedwa ngati tirigu,
ine ndikukuwuzani zimene ndamva
ndikukuwuzani Uthenga wochokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,
Mulungu wa Israeli.
Za Chilango cha Edomu
Uthenga wonena za Duma:
Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti,
“Iwe mlonda, usikuwu utha liti?
Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
Mlonda akuyankha kuti,
“Kukucha, koma kudanso.
Ngati ukufuna kufunsa, funsa tsopano;
ndipo ubwerenso udzafunse.”
Za Chilango cha Arabiya
Uthenga wonena za Arabiya:
Inu anthu amalonda a ku Dedani,
amene usiku mumagona mʼzithukuluzi za ku Arabiya,
perekani madzi kwa anthu aludzu.
Inu anthu a ku Tema
perekani chakudya kwa anthu othawa nkhondo.
Iwo akuthawa malupanga,
lupanga losololedwa,
akuthawa uta wokokakoka
ndiponso nkhondo yoopsa.
Zimene Ambuye akunena kwa ine ndi izi: “Chaka chimodzi chisanathe, potsata mmene amawerengera munthu waganyu, ulemerero wonse wa Kedara udzatheratu. Mwa anthu okoka uta, ankhondo a ku Kedara opulumuka adzakhala owerengeka.” Wayankhula ndi Yehova Mulungu wa Israeli.
Za Chilango cha Yerusalemu
Uthenga wonena za Chigwa cha Masomphenya:
Kodi chachitika nʼchiyani,
kuti nonsenu mukwere pa madenga?
Iwe mzinda wodzaza ndi chisangalalo chodzaza tsaya,
iwe mzinda waphokoso ndi wosokonekera?
Anthu ako ophedwa aja sanaphedwe ndi lupanga,
kapena kufera pa nkhondo.
Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi;
koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe.
Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo,
ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga;
ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa.
Musayesere kunditonthoza
chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione
mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo
mʼChigwa cha Masomphenya.
Malinga agumuka,
komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
Ankhondo a ku Elamu anadza pa magaleta
ndi akavalo ali ndi mivi mʼmanja.
Ankhondo a ku Kiri anakonzeka ndi zishango.
Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta,
ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
zonse zoteteza Yuda zachotsedwa.
Ndipo tsiku limenelo munayangʼanayangʼana
zida zankhondo zomwe zinali mʼnyumba yaufumu ya nkhalango;
inu munaona kuti makoma ambiri a mzinda wa Davide
anali ndi malo ambiri ogumuka;
munasunga madzi
mu chidziwe chakumunsi.
Munawerenga nyumba zonse za mu Yerusalemu
ndipo munagwetsa nyumba zina kuti mulimbitse linga logumuka lija.
Pakati pa makoma awiri munamanga chitsime
chosungiramo madzi ochokera ku dziwe lakale,
koma inu simunadalire Mulungu amene anapanga zimenezi,
kapena kusamalako za Iye amene anazilenga kale lomwe.
Pa tsiku limenelo, Ambuye Yehova Wamphamvuzonse
anakuyitanani kuti mulire ndi kukhetsa misozi;
kumeta mutu wanu mpala
ndi kuvala ziguduli.
Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala;
munapha ngʼombe ndi nkhosa;
munadya nyama ndi kumwa vinyo.
Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa
pakuti mawa tifa!”
Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
Chimene Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse akuti,
“Pita, ukanene kwa Sabina kapitawo,
amene amayangʼanira nyumba yaufumu:
Kodi ukuchita chiyani kuno, nanga ndani anakupatsa chilolezo
kuti udzikumbire manda kuno,
kudzikumbira manda pa phiri
ndi kudzisemera malo opumulira mʼthanthwe?
“Samalira, Yehova watsala pangʼono kukugwira zolimba
ndi kukuponya mwamphamvu, iwe munthu wamphamvu.
Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira
ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu.
Kumeneko ndiko ukafere
ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako.
Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
Ine ndidzakuchotsa pa ukapitawo wako
ndipo ndidzakutsitsa pa udindo wako.
“Tsiku limenelo ndidzayitanitsa mtumiki wanga, Eliyakimu mwana wa Hilikiya. Ndidzamuveka mkanjo wako ndi kumangira lamba wako mʼchiwuno mwake ndi kumupatsa ulamuliro wako. Iye adzakhala kholo la amene amakhala mu Yerusalemu ndiponso a fuko la Yuda. Ndidzamupatsa ulamuliro wa banja la Davide. Adzatsekula ndipo palibe adzatseke, adzatseka popanda wina kutsekula. Ufumu wake udzakhala wokhazikika ngati chikhomo chokhomedwa pa malo olimba. Anthu adzalemekeza nyumba ya abale ake chifukwa cha iye. Ana ndi abale a nyumba ya abambo ake adzakhala ngati katundu pa iye ngati ziwiya zopanda ntchito zimene zapachikidwa pa chikhomo.
“Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
Za Chilango cha Turo
Uthenga wonena za Turo:
Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi:
pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa
ndipo mulibe nyumba kapena dooko.
Zimenezi anazimva
pochokera ku Kitimu.
Khalani chete inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja,
inu amalonda a ku Sidoni,
iwe amene unalemera ndi anthu oyenda pa nyanja.
Pa nyanja zazikulu
panabwera tirigu wa ku Sihori;
zokolola za ku Nailo, ndipo munachita malonda
ndi anthu a mitundu ina.
Chita manyazi, iwe Sidimu
pakuti nyanja yayankhula, linga la ku nyanja (Turo) layankhula kuti,
“Sindinamvepo zowawa za kubereka kapena kuberekapo mwana;
sindinalerepo ana aamuna kapena kulera ana aakazi.”
Mawuwa akadzamveka ku Igupto,
iwo adzachita mantha akadzamva kuti Turo wawonongeka.
Wolokerani ku Tarisisi,
lirani mofuwula, inu anthu okhala mʼmbali mwa nyanja.
Kodi uwu si mzinda wachisangalalo uja,
mzinda wakalekale,
umene anthu ake ankapita
kukakhala ku mayiko akutali?
Kodi ndani anakonza zimenezi kuti zigwere Turo, mzinda umene unakhazikitsa mizinda ina,
mzinda umene amalonda ake ndi akalonga
ndi otchuka
pa dziko lapansi?
Yehova Wamphamvuzonse anakonza zimenezi
kuti athetse kunyada kwawo
ndi kutsitsa anthu otchuka a pa dziko lapansi.
Mubalalike mʼdziko mwanu ngati mtsinje wa Nailo
inu anthu a ku Tarisisi,
pakuti mulibenso chokutetezani.
Yehova watambasula dzanja lake kuloza ku nyanja
ndipo wagwedeza maufumu ake.
Iye walamula kuti Kanaani
agwetse malinga ake.
Iye anati, “Simudzakondwanso konse,
inu anthu opanikizidwa a ku Sidoni, tsopano wamphwanyidwa!
“Ngakhale muwolokere ku Kitimu,
kumeneko simukapezako mpumulo.”
Onani dziko la Ababuloni,
anthu amenewa tsopano atheratu!
Asiriya asandutsa Turo kukhala
malo a zirombo za ku chipululu;
anamanga nsanja zawo za nkhondo,
anagumula malinga ake
ndipo anawasandutsa bwinja.
Lirani mofuwula, inu anthu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi;
chifukwa malinga ako agwetsedwa!
Pa nthawi imeneyo Turo adzayiwalika pa zaka 70, amene ndi masiku a moyo wa mfumu. Koma potsiriza pa zaka 70 zimenezi, Turo adzakhala ngati mkazi wachiwerewere woyimbidwa mu nyimbo:
“Tenga zeze wako uzungulire mzinda,
iwe mkazi wachiwerewere woyiwalika;
imba zeze mokometsera, imba nyimbo zambiri,
kuti anthu akukumbukire.”
Pakutha pa zaka 70, Yehova adzachitapo kanthu pa Turo. Iye adzabwerera ku ntchito yake yakale monga mkazi wachiwerewere ndipo adzachita zachiwerewere ndi maufumu onse a dziko lapansi. Koma phindu lake ndi malipiro ake adzazipereka kwa Yehova; sadzazikundika kapena kuzisunga. Phindu lake lidzapita kwa mtumiki wa Yehova kuti agule zakudya zambiri ndi zovala zokongola.
Chilango cha Yehova pa Dziko Lapansi
Taonani, Yehova adzawononga dziko lapansi
ndi kulisandutsa chipululu;
Iye adzasakaza maonekedwe ake
ndi kumwaza anthu ake onse.
Aliyense zidzamuchitikira mofanana:
wansembe chimodzimodzi munthu wamba,
antchito aamuna mofanananso ndi ambuye awo aamuna,
antchito aakazi chimodzimodzi ambuye awo aakazi,
wogula chimodzimodzi wogulitsa,
wobwereka chimodzimodzi wobwereketsa,
okongola chimodzimodzi okongoza.
Dziko lapansi lidzawonongedwa kwathunthu
ndi kusakazikiratu.
Yehova wanena mawu awa.
Dziko lapansi likulira ndipo likufota,
dziko lonse likuvutika ndipo likuwuma,
anthu omveka a dziko lapansi akuvutika.
Anthu ayipitsa dziko lapansi;
posamvera malangizo ake;
pophwanya mawu ake
ndi pangano lake lamuyaya.
Nʼchifukwa chake matemberero akuwononga dziko lapansi;
anthu a mʼdzikomo akuzunzika chifukwa cha kulakwa kwawo,
iwo asakazika
ndipo atsala ochepa okha.
Vinyo watsopano watha ndipo mphesa zikufota;
onse okonda zosangalatsa ali ndi chisoni.
Kulira kokometsera kwa matambolini kwatha,
phokoso la anthu osangalala latha,
zeze wosangalatsa wati zii.
Anthu sadzayimbanso akumwa vinyo;
akadzamwa zaukali zidzakhala zowawa mʼkamwa mwawo.
Mzinda wachisokonezo uja wawonongeka;
nyumba iliyonse yatsekedwa.
Anthu akulira mʼmisewu kufuna vinyo;
chimwemwe chonse chatheratu,
palibenso chisangalalo pa dziko lapansi.
Mzinda wasanduka bwinja
zipata zake zagumuka.
Zimenezi ndizo zidzachitikire mitundu yonse ya dziko lapansi
ndiponso pakati pa mitundu ya anthu.
Zidzakhala ngati pamene mitengo ya olivi yayoyoledwa,
kapena ngati nthawi ya kunkha la mphesa atatsiriza kukolola.
Koma otsala onse akufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe;
anthu akumadzulo akutamanda ukulu wa Yehova.
Nʼchifukwa chake inu akummawa, tamandani Yehova;
ndi inu okhala mʼmphepete mwa nyanja kwezani dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli.
Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi tikumva kuyimba kotamanda
“Wolungamayo.”
Koma ine ndinati, “Ndatheratu, ndatheratu!
Tsoka kwa ine!
Anthu achinyengo akupitirizabe kuchita zachinyengo,
inde chinyengo chawo chikunkerankera mʼtsogolo.”
Inu anthu adziko lapansi, zoopsa, dzenje
ndi msampha zikukudikirani.
Aliyense wothawa phokoso la zoopsa
adzagwa mʼdzenje;
ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo
adzakodwa ndi msampha.
Zitseko zakumwamba zatsekulidwa,
ndipo maziko a dziko lapansi agwedezeka.
Dziko lapansi lathyokathyoka,
ndipo lagawika pakati,
dziko lapansi lagwedezeka kotheratu.
Dziko lapansi likudzandira ngati munthu woledzera
likugwedezeka ndi mphepo ngati chisimba;
lalemedwa ndi machimo ake.
Lidzagwa ndipo silidzadzukanso.
Tsiku limenelo Yehova adzalanga
amphamvu a kumwamba
ndiponso mafumu apansi pano.
Mulungu adzawasonkhanitsa pamodzi
ngati amʼndende amene ali mʼdzenje.
Adzawatsekera mʼndende
ndipo adzalangidwa patapita nthawi yayitali.
Mwezi udzanyazitsidwa, dzuwa lidzachita manyazi;
pakuti Yehova Wamphamvuzonse adzakhala mfumu ndipo adzalamulira;
pa Phiri la Ziyoni ndi ku Yerusalemu,
ndipo adzaonetsa ulemerero wake pamaso pa akuluakulu.
Nyimbo Yotamanda Yehova
Yehova ndinu Mulungu wanga;
ine ndidzakukwezani ndi kutamanda dzina lanu,
pakuti mwachita zodabwitsa
zimene munakonzekeratu kalekale
mokhulupirika kwambiri.
Inu mwasandutsa mzinda uja kukhala mulu wamiyala.
Ndipo mzinda wamalinga wasanduka bwinja,
linga la anthu achilendo lero si mzindanso
ndipo sidzamangidwanso.
Nʼchifukwa chake anthu amphamvu adzakulemekezani;
mizinda ya mitundu ya anthu ankhanza idzakuopani.
Inu mwakhala ngati populumukira pa anthu osauka,
mwakhala ngati kobisalirako munthu wovutika pa nthawi ya masautso ake.
Mwakhala ngati pobisalirapo
pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mthunzi pa nthawi ya dzuwa.
Pakuti anthu ankhanza
ali ngati mphepo yamkuntho yowomba pa khoma,
ndiponso ngati kutentha mʼdziko lowuma.
Inu mumaletsa phokoso la anthu achilendo.
Monga momwe mthunzi wa mtambo umachepetsa kutentha,
inu munaletsa nyimbo za anthu ankhanza.
Pa phiri ili Yehova Wamphamvuzonse adzakonzera
anthu a mitundu yonse madyerero a zakudya zokoma ndi vinyo wabwino.
Phwando la nyama yonona
ndi vinyo wabwino kwambiri.
Iye adzachotsa kulira
kumene kwaphimba anthu ngati nsalu.
Adzachotsa chinsalu chimene chakuta mitundu yonse ya anthu.
Yehova adzathetsa imfa mpaka muyaya,
Ambuye Yehova adzapukuta misozi mʼmaso
mwa munthu aliyense;
adzachotsa manyazi a anthu ake
pa dziko lonse lapansi,
Yehova wayankhula.
Tsiku limenelo iwo adzati,
“Ndithudi, uyu ndiye Mulungu wathu;
ife tinamudalira ndipo anatipulumutsa.
Uyu ndiye Yehova, ife tinamudalira;
tiyeni tikondwe ndi kusangalala chifukwa watipulumutsa.”
Yehova adzateteza phiri limeneli ndi dzanja lake;
ndipo Amowabu adzawapondereza pomwe alilipo,
ngati mmene amapondera manyowa mʼdzenje.
Amowabuwo adzatambasula manja awo mʼmenemo,
ngati mmene amachitira munthu wosambira.
Koma Mulungu adzathetsa kunyada kwawo
ngakhale luso la manja awo.
Iye adzagumula malinga awo ataliatali
ndipo adzawagwetsa
ndi kuwaponya pansi,
pa fumbi penipeni.
Nyimbo ya Matamando
Tsiku limenelo anthu a mʼdziko la Yuda adzayimba nyimbo iyi.
Tili ndi mzinda wolimba.
Mulungu amawuteteza ndi zipupa
ndi malinga.
Tsekulani zipata za mzinda
kuti mtundu wolungama
ndi wokhulupirika ulowemo.
Inu mudzamupatsa munthu
wa mtima wokhazikika
mtendere weniweni.
Mudalireni Yehova mpaka muyaya,
chifukwa Yehova Mulungu ndiye Thanthwe losatha.
Iye amatsitsa anthu amene amadziyika pamwamba,
iye amagwetsa pansi mzinda wodzitukumula,
amagumula makoma ake
ndi kuwagwetsa pansi pa fumbi penipeni.
Mapazi a anthu akuwupondereza,
mapazi a anthu oponderezedwa,
mapazi anthu osauka.
Njira ya munthu wolungama ndi yosalaza,
Inu Wolungamayo, mumasalaza njira ya wolungama.
Inde Yehova, timayenda mʼnjira zanu zolungama,
ife timayembekezera Inu;
mitima yathu imakhumba kukumbukira
ndi kulemekeza dzina lanu.
Moyo wanga umalakalaka Inu usiku wonse;
nthawi yammawa ndimafunafuna Inu.
Pamene muweruza dziko lapansi
anthu amaphunzira kuchita chilungamo.
Ngakhale mukomere mtima anthu oyipa,
saphunzira chilungamo.
Amachita zoyipa mʼdziko la chilungamo,
ndipo sazindikira ululu wa Yehova.
Inu Yehova, mwatukula dzanja lanu kuti muwalange,
koma iwo sakuliona dzanjalo.
Aloleni anthu aone ndi kuchita manyazi poona mmene mukondera anthu anu;
ndipo moto umene mwasonkhera adani anu uwapsereze.
Yehova, mumatipatsa mtendere;
ndipo zonse zimene ife tinazichita munatichitira ndinu.
Inu Yehova Mulungu wathu, ngakhale takhala tikulamulidwa ndi ena mʼmalo mwanu,
koma ife timalemekeza dzina lanu lokha.
Iwo tsopano sadzadzukanso;
mizimu yawo sidzabwera kudzativutitsa
pakuti mwawalanga ndipo mwawawononga;
palibenso amene amawakumbukira.
Inu Yehova, mwaukulitsa mtundu wathu;
mwauchulukitsa ndithu
ndipo mwalandirapo ulemu;
mwaukuza mbali zonse za dziko.
Yehova, anthu anu anabwera kwa Inu pamene anali mʼmasautso;
pamene munawalanga,
iwo anapemphera kwa Inu.
Monga mayi woyembekezera pamene nthawi yake yobereka yayandikira
amamva kupweteka ndipo amalira ndi ululu,
ifenso tinali chimodzimodzi pamaso panu, Inu Yehova.
Ife chimodzimodzi tinamva ululu, ngati mayi pa nthawi yobala mwana,
koma sitinapindulepo kanthu,
kapena kupulumutsa dziko lapansi;
sitinabadwitse anthu atsopano pa dziko pano.
Koma anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo;
matupi awo adzadzuka.
Iwo amene ali ku fumbi tsopano
adzadzuka ndi kuyimba mosangalala.
Monga mame amafewetsa pansi kutsitsimutsa zomera,
momwenso Yehova adzaukitsa anthu amene anafa kale.
Abale anga, pitani mukalowe mʼnyumba zanu
ndipo mukadzitsekere;
mukabisale kwa kanthawi kochepa
mpaka ukali wake utatha.
Taonani, Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala;
akubwera kudzalanga anthu a dziko lapansi chifukwa cha machimo awo.
Dziko lapansi lidzawulula magazi amene anakhetsedwa pa dzikolo;
dziko lapansi silidzabisanso mitembo ya anthu ophedwa.
Za Munda Wamphesa wa Yehova
Tsiku limenelo,
Yehova ndi lupanga lake
lakuthwa, lalikulu ndi lamphamvu,
adzalanga Leviyatani chinjoka chothawa chija,
Leviyatani chinjoka chodzikulunga;
adzapha chirombo choopsa cha mʼnyanja.
Tsiku limenelo Yehova adzati,
“Tidzayimba nyimbo ya munda wamphesa wobereka bwino:
Ine, Yehova, ndimawuyangʼanira;
ndimawuthirira nthawi zonse.
Ndimawulondera usana ndi usiku
kuti wina angawononge.
Ine sindinakwiye.
Ngati mkandankhuku ndi minga zikanaoneka ndikanalimbana nazo!
Ndikachita nazo nkhondo;
ndikanazitentha zonse ndi moto.
Koma ngati apo ayi, abweretu kwa Ine adani angawo kuti ndidzawateteze;
apangane nane za mtendere,
ndithu, apangane nane za mtendere.”
Masiku akubwerawo Yakobo adzazika mizu,
Israeli adzaphukira ndi kuchita maluwa,
ndipo adzadzaza dziko lonse lapansi ndi zipatso.
Kodi Yehova anakantha Israeli
ngati momwe anakanthira anthu amene anazunza Israeli?
Kapena kodi Yehova anapha Israeli
ngati mmene anthu ena anaphera Israeli?
Yehova mwawalanga powapirikitsa ndi kuwatumiza ku ukapolo,
mwawachotsa ndi mpweya wanu woopsa,
monga zimachitikira pa tsiku la mkuntho wochokera kummawa.
Yehova adzakhululuka kulakwa kwa Yakobo.
Iwo adzaonetsa kuti alapadi pamene adzaphwanya miyala yonse ya guwa lachikunja,
ngati mmene anthu amaphwanyira miyala yanjereza
mpaka kukhala ngati fumbi lokhalokha.
Sipadzapezekanso mafano a Asera
kapena maguwa ofukiza lubani.
Mzinda wamalinga uja wasanduka bwinja,
wasanduka malo osiyidwa, ndi kutayidwa ngati chipululu;
kumeneko amadyetselako ana angʼombe
kumeneko zimapumulako ziweto
ndi kumwetula nthambi za mitengo kotheratu.
Pamene nthambi za mitengoyo zauma, zimathyoka
ndipo amayi amabwera nazitola ndi kuzisandutsa nkhuni.
Pakuti awa ndi anthu opanda nzeru;
kotero Mulungu amene anawapanga sadzachitira chisoni,
ndipo Mlengi wawo sawakomera mtima.
Tsiku limenelo Yehova adzasonkhanitsa pamodzi anthu ake mmodzimmodzi kumalo opunthira tirigu, kuchokera ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku mtsinje wa ku Igupto. Ndipo tsiku limenelo lipenga lalikulu lidzalira. Amene akuzunzika ku Asiriya iwo amene ali ku ukapolo ku Igupto adzabwera ndi kudzalambira Yehova pa phiri lopatulika mu Yerusalemu.
Tsoka kwa Efereimu
Tsoka ufumu wonyada wa zidakwa za ku Efereimu.
Tsoka kwa ulemerero wake wokongola umene ukufota ngati duwa
limene lili pa mutu pa anthu
oledzera a mʼchigwa chachonde.
Taonani, ambuye ali naye wina wamphamvu ndi nyonga.
Iye adzabwera ngati mkuntho wamatalala ndi namondwe wowononga,
ngati madzi amphamvu osefukira a mvula yamkuntho;
ndipo adzawagwetsa pansi mwankhanza.
Ulamuliro wa atsogoleri oledzera
a ku Efereimu adzawuthetsa.
Ndipo ulemerero wokongola wa mzinda umene uli ngati duwa
lofota pamutu pa anthu oledzera a mʼchigwa chachonde uja,
udzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kupsa
imene munthu akangoyiona amayithyola
nthawi yokolola isanakwane.
Tsiku limenelo Yehova Wamphamvuzonse
adzakhala ngati nkhata yaufumu,
chipewa chokongola
kwa anthu ake otsala.
Iye adzapereka mtima
wachilungamo kwa oweruza,
adzakhala chilimbikitso kwa
amene amabweza adani pa zipata za mzinda.
Nawonso awa ali dzandidzandi chifukwa cha vinyo
ndipo akusochera chifukwa cha mowa:
ansembe ndi aneneri akudzandira chifukwa cha mowa
ndipo akusokonezeka chifukwa cha vinyo;
akusochera chifukwa cha mowa,
akudzandira pamene akuona masomphenya,
kupunthwa pamene akupereka chigamulo.
Pa matebulo onse pali masanzi okhaokha
ndipo palibenso malo wopanda zonyansa.
Iwo akuti, “Kodi munthu ameneyu akufuna aphunzitse ndani?
Uthengawu akufuna kufotokozera yani?
Ndi kwa ana amene aleka kuyamwa,
kwa makanda ongowachotsa kumene ku bere?
Akuyesa kumatiphunzitsa pangʼonopangʼono
lemba ndi lemba, mzere ndi mzere,
phunziro ndi phunziro.
Zonsezi akungoti apa pangʼono apa pangʼono.”
Mulungu adzayankhula kwa anthu ake kudzera mwa anthu aziyankhulo zachilendo, ziyankhulo zosamveka bwino.
Mulungu adzayankhula kwa anthu awa, amene
anakuwuzani kuti,
“Malo opumulira ndi ano,
otopa apumule, malo owusira ndi ano.”
Koma inu simunamvere.
Choncho Yehova adzakuphunzitsani
pangʼonopangʼono lemba ndi lemba,
mzere ndi mzere, phunziro ndi phunziro.
Kotero mudzayenda ndi kugwa chambuyo,
adzapweteka ndi kukodwa mu msampha
ndipo adzakutengani ku ukapolo.
Nʼchifukwa chake imvani mawu a Yehova,
inu anthu achipongwe amene mumalamulira anthu awa mu Yerusalemu.
Inu mumayankhula monyada kuti, “Ife tinachita pangano ndi imfa,
ife tachita mgwirizano ndi manda.
Pamene mliri woopsa ukadzafika
sudzatikhudza ife,
chifukwa timadalira bodza ngati pothawirapo pathu
ndi chinyengo ngati malo anthu obisalapo.”
Tsono zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi:
“Taonani, ndikuyika mwala wovomerezeka ndi amisiri
ngati maziko mu Ziyoni,
mwala wapangodya, wamtengowapatali wopanga maziko amphamvu;
munthu amene awukhulupirira sadzagwedezeka.
Ntchito zolungama zidzakhala ngati chingwe choyezera maziko ake,
ndipo chilungamo chidzakhala chowongolera mzere;
matalala adzawononga malo anu othawirapo, amene ndi mabodza,
ndipo madzi adzamiza malo anu obisalako.
Pangano limene munachita ndi imfa lidzathetsedwa;
mgwirizano wanu ndi manda udzachotsedwa.
Pakuti mliri woopsa udzafika,
ndipo udzakugonjetsani.
Ndipo ukadzangofika udzakutengani.
Udzafika mmawa uliwonse,
usiku ndi usana.”
Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu
adzaopsedwa kwambiri.
Mudzakhala ngati munthu wogona pa bedi lalifupi kwambiri kuti sangathe kutambalitsapo miyendo;
ndiponso mudzakhala ngati munthu amene wafunda bulangeti lochepa kwambiri kuti sangathe nʼkufunda komwe.
Yehova adzamenya nkhondo monga anachitira ku phiri la Perazimu
adzakalipa monga anachitira ku chigwa cha Gibiyoni;
adzagwira ntchito yake yooneka ngati yachilendo,
ndipo zimene ati adzachite zidzakhala ngati zodabwitsa.
Tsopano lekani kunyoza,
mukapanda kutero maunyolo anu adzakuthinani kwambiri;
Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse wandiwuza kuti,
“Ndagamula kuti ndidzawononga dziko lapansi.”
Tcherani khutu ndipo mumve mawu anga;
mvetserani ndipo mumve zimene ndikunena.
Kodi mlimi wofuna kudzala mbewu amangokhalira kutipula kokhakokha?
Kodi amangokhalira kugawula ndi kugalawuza kokhakokha?
Pamene iye wasalaza mundawo,
kodi samafesa mawere ndi chitowe?
Kodi suja samadzala tirigu
ndi barele mʼmizere yake,
nadzala mchewere mʼphepete mwa mundawo?
Mulungu wake amamulangiza
ndi kumuphunzitsa njira yabwino.
Mawere sapunthira chopunthira cha galeta lopanda mikombero,
kapena chitowe sapuntha popondetsapo mikombero ya galeta;
mawere amapuntha ndi ndodo
ndipo chitowe amapuntha ndi kamtengo.
Tirigu ayenera kusinjidwa kuti apangire buledi,
komabe munthu samangokhalira kupuntha tiriguyo osalekeza, kuopa kuti angatekedzeke.
Ngakhale kuti amapuntha tiriguyo poyendetsapo mikombero ya galeta,
koma akavalo ake satekedza tiriguyo.
Izinso zimachokera kwa Yehova Wamphamvuzonse,
wa uphungu wodabwitsa ndi wa nzeru zopambana.
Tsoka kwa Mzinda wa Davide
Tsoka kwa iwe, Arieli, Arieli,
mzinda umene Davide anakhazikitsamo zithando za nkhondo!
Papite chaka chimodzi kapena ziwiri
ndipo masiku a zikondwerero zanu azipitirirabe ndithu.
Komatu Ine ndidzathira nkhondo Arieli
ndipo kudzakhala kulira ndi kudandaula,
mzindawo udzasanduka ngati ngʼanjo ya guwa lansembe.
Ine ndidzamanga misasa ya nkhondo kulimbana ndi mzindawo;
ndidzakuzungulira ndi nsanja za nkhondo
ndi kumanga mitumbira yanga ya nkhondo kulimbana nawe.
Utagwetsedwa pansi, iwe udzayankhula kuchokera mʼnthaka,
mawu ako adzatuluka uli mʼfumbi,
adzamveka ngati a mzukwa.
Mawu ako adzamveka ngati onongʼona kuchokera mʼfumbi.
Koma chigulu cha adani ako chidzasanduka chifwirimbwiti.
Chigulu cha ankhondo achilendo chidzabalalika ngati mungu wowuluzika ndi mphepo.
Mwadzidzidzi ndi mosayembekezereka,
Yehova Wamphamvuzonse adzabwera
ndi mabingu ndi chivomerezi ndi phokoso lalikulu,
kamvuluvulu ndi namondwe ndi malawi a moto wonyeketsa.
Tsono chigulu chankhondo cha mitundu ina yonse chimene chikulimbana ndi mzinda wa Arieli
nʼkumathira nkhondo mzindawo, malinga ake ndi kuwuzinga,
chigulu chonsecho chidzazimirira ngati maloto,
gati zinthu zoziona mʼmasomphenya usiku.
Chidzakhala ngati munthu wanjala wolota akudya,
koma podzuka ali nayobe njala;
kapena ngati munthu waludzu wolota akumwa,
koma podzuka, ali nalobe ludzu, kummero kwake kuli gwaa.
Izi zidzachitika pamene chigulu cha nkhondo cha mitundu ina yonse
chikunthira nkhondo Phiri la Ziyoni.
Pitirizani kuledzera ndipo mudzakhala opusa.
Dzitsekeni mʼmaso ndipo mukhale osapenya,
ledzerani, koma osati ndi vinyo,
dzandirani, koma osati ndi mowa.
Yehova wakugonetsani tulo tofa nato.
Watseka maso anu, inu aneneri;
waphimba mitu yanu, inu alosi.
Kwa inu mawu onsewa ali ngati buku lotsekedwa, ndipo ngati lipatsidwa kwa wina wodziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde tawerengani bukuli,” iye adzati, “Sindingathe popeza ndi lomatidwa.” Kapena ngati lipatsidwa kwa amene sadziwa kuwerenga ndi kunena kuti, “Chonde werenga bukuli,” iye adzayankha kuti, “Ine sindidziwa kuwerenga.”
Ambuye akuti,
“Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo,
ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo,
koma mitima yawo ili kutali ndi Ine.
Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso.
Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.
Nʼchifukwa chakenso Ine ndidzapitirira
kuwachitira ntchito zodabwitsa;
nzeru za anthu anzeru zidzatha,
luntha la anthu aluntha Ine ndidzalinyoza.”
Tsoka kwa amene amayesetsa
kubisira Yehova maganizo awo,
amene amachita ntchito zawo mu mdima nʼkumanena kuti,
“Ndani amene akundiona kapena ndani akudziwa zimene ndikuchita?”
Inu mumazondotsa zinthu
ngati kuti dothi lasanduka wowumba mbiya.
Kodi chinthu chopangidwa chingawuze wochipanga kuti
“Sunandipange ndi iwe?”
Kapena mʼphika kunena kwa amene anawuwumba kuti,
“Iwe sudziwa chilichonse?”
Kodi Lebanoni posachedwapa sadzasanduka munda wachonde,
ndipo kodi munda wachondewo ngati nkhalango?
Tsiku limenelo anthu osamva adzamva mawu a mʼbuku,
ndipo anthu osaona amene
ankakhala mu mdima adzapenya.
Anthu odzichepetsa adzakhalanso ndi chimwemwe mwa Yehova;
ndipo anthu osowa adzakondwa chifukwa cha Woyerayo wa Israeli.
Koma anthu ankhanza adzazimirira,
oseka anzawo sadzaonekanso,
ndipo onse okopeka ndi zoyipa adzawonongedwa.
Yehova adzalanga amene amasinjirira munthu kuti apezeke wolakwa,
kapena kuphophonyetsa anthu ozenga mlandu
ndi umboni wonama kuti osalakwa asaweruzidwe mwachilungamo.
Choncho Yehova amene anawombola Abrahamu, akunena kwa zidzukulu za Yakobo kuti,
“Anthu anga sadzachitanso manyazi;
nkhope zawo sizidzagwanso ndi manyazi.
Akadzaona ana awo ndi
ntchito ya manja anga pakati pawo,
adzatamanda dzina langa loyera;
adzazindikira kuyera kwa Woyerayo wa Yakobo,
ndipo adzachita naye mantha Mulungu wa Israeli.
Anthu opusa adzapeza nzeru;
onyinyirika adzalandira malangizo.”
Tsoka kwa Mtundu Wopanduka
Yehova akuti, “Tsoka kwa ana ondipandukira
amene amachita zowakomera iwo okha osati Ine,
nachita mgwirizano wawowawo
koma osati motsogozedwa ndi Ine.
Choncho amanka nachimwirachimwira.
Amapita ku Igupto kukapempha thandizo
koma osandifunsa;
amathawira kwa Farao kuti awateteze,
ku Igupto amafuna malo opulumulira.
Koma chitetezo cha Farao chidzakhala manyazi anu,
malo a mthunzi a ku Igupto mudzachita nawo manyazi.
Ngakhale kuti nduna zawo zili ku Zowani,
ndipo akazembe awo afika kale ku Hanesi,
aliyense wa ku Yuda adzachita manyazi
chifukwa cha anthu opanda nawo phindu,
amene sabweretsa thandizo kapena phindu,
koma manyazi ndi mnyozo.”
Uthenga wonena za nyama za ku Negevi:
Akazembe akuyenda mʼdziko lovuta ndi losautsa,
mʼmene muli mikango yayimuna ndi yayikazi,
mphiri ndi njoka zaululu.
Iwo amasenzetsa abulu ndi ngamira chuma chawo,
kupita nazo kwa mtundu wa anthu
umene sungawathandize.
Amapita ku Igupto amene thandizo lake ndi lachabechabe.
Nʼchifukwa chake dzikolo ndalitcha
Rahabe chirombo cholobodoka.
Yehova anandiwuza kuti, “Tsopano pita,
ukalembe zimenezi mʼbuku iwo akuona
ndipo lidzakhala ngati umboni wosatha
masiku a mʼtsogolo.
Amenewa ndi anthu owukira, onama ndi
osafuna kumvera malangizo a Yehova.
Iwo amawuza alosi kuti,
‘Musationerenso masomphenya!’
Ndipo amanena kwa mneneri kuti,
‘Musatinenerenso zoona,’
mutiwuze zotikomera,
munenere za mʼmutu mwanu.
Patukani pa njira ya Yehova,
lekani kutsata njira ya Yehova;
ndipo tisamvenso mawu
a Woyerayo uja wa Israeli!”
Nʼchifukwa chake Woyerayo wa Israeli akunena kuti,
“Popeza inu mwakana uthenga uwu,
mumakhulupirira zopondereza anzanu
ndipo mumadalira kuchita zoyipa,
choncho tchimo linalo lidzakhala ngati mingʼalu
pa khoma lalitali ndi lopendama
limene linagwa mwadzidzidzi ndi mwamsangamsanga.
Lidzaphwanyika ngati mbiya
imene yanyenyekeratu,
mwakuti pakati pake sipadzapezeka phale ngakhale
lopalira moto mʼngʼanjo
kapena lotungira madzi mʼchitsime.”
Zimene Ambuye Yehova, Woyerayo wa Israeli ananena ndi izi:
“Ngati mubwerera ndi kupuma mudzapulumuka,
ngati mukhala chete ndi kukhulupirira mudzakhala amphamvu,
koma inu munakana zimenezi.
Inu mukuti, ‘Ayi ife tidzathawa,
tidzakwera pa akavalo aliwiro.’
Zoonadi kuti mudzakwera pa akavalo aliwiro,
koma okuthamangitsani adzakhalanso aliwiro.
Anthu 1,000 mwa inu adzathawa
poona mdani mmodzi;
poona adani asanu okha
nonsenu mudzathawa.
Otsala anu
adzakhala ngati mbendera pa phiri,
ndi ngati chizindikiro cha pa chulu.”
Komatu Yehova akufunitsitsa kuti akukomereni mtima,
iye ali wokonzeka kuti akuchitireni chifundo.
Pakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo.
Ndi odala onse amene amakhulupirira Iye!
Inu anthu a ku Ziyoni, amene mukhala mu Yerusalemu simudzaliranso. Mulungu adzakukomerani mtima pamene adzamva kulira kwanu kopempha thandizo! Ndipo akadzamva, adzakuyankhani. Ngakhale Ambuye adzakulowetseni mʼmasautso, aphunzitsi anu sadzakhala kakasi; inu mudzawaona ndi maso anuwo. Ngati mudzapatukira kumanja kapena kumanzere, mudzamva mawu kumbuyo kwanu woti, “Njira ndi iyi; yendani mʼmenemo.” Pamenepo mudzawononga mafano anu okutidwa ndi siliva ndiponso zifanizo zanu zokutidwa ndi golide; mudzawataya ngati zinthu zonyansa ndipo mudzati, “Zichoke zonsezi!”
Yehova adzakugwetseraninso mvula pa mbewu zanu zimene mukadzale mʼnthaka, ndipo chakudya chimene mudzakolole chidzakhala chabwino ndi chochuluka. Tsiku limenelo ngʼombe zanu zidzadya msipu wochuluka. Ngʼombe ndi abulu amene amalima mʼmunda adzadya chakudya chamchere, chopetedwa ndi foloko ndi fosholo. Pa tsiku limene adani anu adzaphedwa ndi nsanja zawo kugwa, mitsinje ya madzi idzayenda pa phiri lililonse lalikulu ndi pa phiri lililonse lalingʼono. Mwezi udzawala ngati dzuwa, ndipo kuwala kwa dzuwa kudzawonjezereka kasanu nʼkawiri, ngati kuwala kwa tsiku limodzi. Yehova adzamanga mabala a anthu ake ndi kupoletsa zilonda zimene Iye anachititsa polanga anthu ake.
Taonani, Yehova akubwera kuchokera kutali,
ndipo mkwiyo wake ndiwonyeka ndi chiweruzo chake chidzakhala chopweteka.
Iye wayankhula mwaukali kwambiri,
ndipo mawu ake ali ngati moto wonyeka.
Mpweya wake uli ngati mtsinje wosefukira,
wa madzi ofika mʼkhosi.
Iye adzasefa anthu a mitundu ina ndi sefa wosakaza;
Iye akuyika zitsulo mʼkamwa mwa anthu a mitundu ina ngati akavalo,
kuti ziwasocheretse.
Ndipo inu mudzayimba
mokondwa monga mumachitira usiku pa chikondwerero chopatulika.
Mudzasangalala
ngati anthu oyimba zitoliro
popita ku phiri la Yehova,
thanthwe la Israeli.
Anthu adzamva liwu la ulemerero la Yehova
ndipo adzaona dzanja lake likutsika pa iwo
ndi mkwiyo woopsa, pamodzi ndi moto wonyeketsa,
mphenzi, namondwe ndi matalala.
Asiriya adzaopa liwu la Yehova,
ndipo Iye adzawakantha ndi ndodo.
Yehova akamadzalanga adani ake ndi ndodo,
anthu ake adzakhala akuvina nyimbo
zoyimbira matambolini ndi azeze,
Yehova ndiye ati adzamenyane ndi Asiriyawo.
Malo otenthera zinthu akonzedwa kale;
anakonzera mfumu ya ku Asiriya.
Dzenje la motolo ndi lozama ndi lalikulu,
ndipo muli nkhuni zambiri;
mpweya wa Yehova,
wangati mtsinje wa sulufule,
udzayatsa motowo pa nkhunizo.
Tsoka kwa Amene Amadalira Igupto
Tsoka kwa amene amapita ku Igupto kukapempha chithandizo,
amene amadalira akavalo,
nakhulupirira kuchuluka kwa magaleta awo ankhondo
ndiponso mphamvu za asilikali awo okwera pa akavalo,
koma sakhulupirira Woyerayo wa Israeli,
kapena kupempha chithandizo kwa Yehova.
Komatu Yehovayo ndi wanzeru ndipo angathe kuwononga,
ndipo sasintha chimene wanena.
Adzalimbana ndi anthu ochita zoyipa,
komanso ndi amene amathandiza anthu ochita zoyipa.
Aigupto ndi anthu chabe osati Mulungu;
akavalo awo ndi nyama chabe osati mizimu.
Yehova akangotambasula dzanja lake,
amene amapereka chithandizo adzapunthwa,
amene amalandira chithandizocho adzagwa;
onsewo adzathera limodzi.
Zimene Yehova akunena kwa ine ndi izi:
“Monga mkango kapena msona wamkango umabangula
ukagwira nyama yake,
ndipo suopsedwa kapena kusokonezeka
ndi kufuwula kwa abusa amene akulimbana nayo,
momwemonso palibe chingaletse
Yehova Wamphamvuzonse
kubwera kudzatchinjiriza
phiri la Ziyoni ndi zitunda zake.
Monga mbalame zowuluka pamwamba pa zisa zake,
Yehova Wamphamvuzonse adzatchinjiriza Yerusalemu;
ndi kumupulumutsa,
iye adzawupitirira ndi kuwulanditsa.”
Inu Aisraeli, bwererani kwa Iye amene munamuwukira kwakukulu. Pakuti tsiku limenelo nonsenu mudzataya mafano anu a siliva ndi golide amene mumapanga ndi manja anu auchimo.
“Aasiriya adzaphedwa ku nkhondo ndi mphamvu osati za munthu.
Lupanga, osati la munthu, lidzawawononga.
Adzathawa ku nkhondo ndipo anyamata awo
adzagwira ntchito yathangata.
Mfumu yawo idzamwalira ndi mantha,
ndipo atsogoleri awo ankhondo adzathawa ndi mantha
kusiya pambuyo mbendera yawo ya nkhondo.”
Akutero Yehova, amene moto wake uli mu Ziyoni,
ndipo ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
Ufumu Wachilungamo
Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo,
ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo
ndi malo obisalirapo namondwe,
adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu,
ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,
ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa,
ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake
ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru,
amaganiza kuchita zoyipa:
Iye amachita zoyipira Mulungu,
ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova;
anjala sawapatsa chakudya
ndipo aludzu sawapatsa madzi.
Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso,
iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa.
Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake
ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino,
Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
Akazi a ku Yerusalemu
Khalani maso, inu akazi
amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji
ndipo imvani mawu anga.
Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
Pakapita chaka ndi masiku pangʼono
inu akazi amatama mudzanjenjemera;
chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika
ndipo zipatso sizidzaoneka.
Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu;
ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu.
Vulani zovala zanu,
ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde,
ndi mphesa yawonongeka.
Mʼdziko la anthu anga
mwamera minga ndi mkandankhuku.
Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero
ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
Nyumba yaufumu idzasiyidwa,
mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu;
malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya.
Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
Yehova adzatipatsa mzimu wake,
ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde,
ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama
ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;
zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere,
mʼnyumba zodalirika,
ndi malo osatekeseka a mpumulo.
Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala
ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
inutu mudzakhala odalitsika ndithu.
Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse,
ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.
Msautso ndi Thandizo
Tsoka kwa iwe, iwe wowonongawe,
amene sunawonongedwepo!
Tsoka kwa iwe, iwe mthirakuwiri,
iwe amene sunanyengedwepo!
Iwe ukadzaleka kuwononga,
udzawonongedwa,
ukadzasiya umʼthirakuwiri, adzakuwononga,
ndipo ukadzaleka kuchita zachinyengo adzakunyenga.
Inu Yehova, mutikomere mtima ife;
tikulakalaka Inu.
Tsiku ndi tsiku mutitchinjirize ndi mkono wanu,
ndipo mutipulumutse pa nthawi ya masautso.
Mukatulutsa liwu lanu longa bingu mitundu ya anthu imathawa;
pamene Inu mwadzambatuka mitundu ya anthu imabalalika.
Zofunkha za ku nkhondo za mitundu ina Aisraeli adzazisonkhanitsa ngati mmene limachitira dzombe.
Iwo adzalumphira zofunkhazo monga mmene limachitira dzombe.
Yehova wakwezeka kwambiri pakuti amakhala pamwamba pa zonse
adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo ndi chipulumutso.
Iye adzakupatsani mtendere pa nthawi yanu,
adzakupatsani chipulumutso chochuluka, nzeru zambiri ndi chidziwitso chochuluka;
kuopa Yehova ngati madalitso.
Taonani, anthu awo amphamvu akulira mofuwula mʼmisewu;
akazembe okhazikitsa mtendere akulira kwambiri.
Mʼmisewu yayikulu mulibe anthu,
mʼmisewu mulibe anthu a paulendo.
Mdaniyo ndi wosasunga pangano.
Iye amanyoza mboni.
Palibe kulemekezana.
Dziko likulira ndipo likunka likutha.
Nkhalango ya Lebanoni ikuchita manyazi, yafota.
Chigwa cha chonde cha Saroni chasanduka chachidalala.
Masamba a mitengo ya ku Basani ndi Karimeli akuyoyoka.
Yehova akunena kuti, “Tsopano ndidzadzambatuka
ndipo ndidzaonetsa mphamvu zanga,
ndipo ndidzakwezedwa.
Zolingalira zanu nʼzachabechabe
ngati udzu wamanyowa.
Mpweya wamoto udzakupserezani.
Anthu a mitundu ina adzatenthedwa ngati miyala ya njereza;
ndi ngati minga yodulidwa.”
Inu amene muli kutali, imvani zimene ndachita;
inu amene muli pafupi, dziwani mphamvu zanga
Mu mzinda wa Ziyoni anthu ochimwa agwidwa ndi mantha;
anthu osapembedza Mulungu akunjenjemera:
Iwo akunena kuti, “Ndani wa ife angathe kukhala mʼmoto wonyeketsa?
Ndani wa ife angathe kukhala moto wosatha?”
Angathe kuti ndi amene amachita zolungama
ndi kuyankhula zoona,
amene amakana phindu lolipeza monyenga
ndipo salola manja ake kulandira ziphuphu,
amene amatseka makutu ake kuti angamve mawu opangana kupha anzawo
ndipo amatsinzina kuti angaone zoyipa.
Munthu wotere ndiye adzakhale pa nsanja,
kothawira kwake kudzakhala mʼmalinga a mʼmapiri.
Azidzalandira chakudya chake
ndipo madzi sadzamusowa.
Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola
ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:
“Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?
Ali kuti wokhometsa misonkho uja?
Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,
anthu aja achiyankhulo chosadziwika,
chachilendo ndi chosamveka.
Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;
maso anu adzaona Yerusalemu,
mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,
zikhomo zake sizidzazulidwa,
kapena zingwe zake kuduka.
Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake
ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.
Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,
sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,
Yehova ndiye wotilamulira,
Yehova ndiye mfumu yathu;
ndipo ndiye amene adzatipulumutse.
Zingwe za sitima zapamadzi za adani athu zamasuka,
sizikutha kulimbitsa mlongoti wake,
matanga ake sakutheka kutambasuka.
Ngakhale tidzagawana zofunkha zochuluka kwambiri
ndipo ngakhale olumala adzatenga zofunkhazo.
Palibe ndi mmodzi yemwe wokhala mʼZiyoni adzanene kuti, “Ndikudwala”
ndipo anthu onse okhala mʼmenemo machimo awo adzakhululukidwa.
Chiweruzo cha Anthu a Mitundu Yonse
Inu anthu a mitundu yonse, bwerani pafupi kuti mumve:
tcherani khutu, inu anthu a mitundu ina yonse:
Limvetsere dziko lapansi pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,
dziko lonse pamodzi ndi zonse zochokera mʼmenemo!
Yehova wayipidwa ndi anthu a mitundu yonse;
wapsera mtima magulu awo onse ankhondo.
Iye adzawawononga kotheratu,
nawapereka kuti aphedwe.
Anthu awo ophedwa adzatayidwa kunja,
mitembo yawo idzawola ndi kununkha;
mapiri adzafiira ndi magazi awo.
Dzuwa, mwezi ndi nyenyezi zidzasungunuka
ndipo mlengalenga mudzakulungidwa ngati chipepala;
nyenyezi zonse zidzayoyoka
ngati masamba ofota a mphesa,
ngati masamba onyala a mtengo wa mkuyu.
Yehova akuti, “Lupanga langa lakhutiratu magazi kumwamba;
taonani, likutsika kudzalanga anthu a ku Edomu,
anthu amene ndawawononga kotheratu.”
Lupanga la Yehova lakhuta magazi,
lakutidwa ndi mafuta;
magazi a ana ankhosa onenepa ndi ambuzi,
mafuta a ku impsyo za nkhosa zazimuna.
Pakuti Yehova ali ndi nsembe mu Bozira
ndiko kuphedwa kwa anthu ambiri mʼdziko la Edomu.
Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso njati,
ngʼombe zazimuna zazingʼono ndi zazikulu zomwe.
Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha,
ndipo nthaka idzakutidwa ndi mafuta.
Iyi ndi nthawi imene Yehova adzalipsira
ndi kulanga adani a Ziyoni.
Madzi a mʼmitsinje ya Edomu adzasanduka phula,
ndipo fumbi lake lidzasanduka sulufule;
dziko lake lidzasanduka phula lamoto!
Motowo sudzazimitsidwa usiku ndi usana;
utsi wake udzafuka kosalekeza.
Dzikolo lidzakhala chipululu pa mibado ndi mibado;
palibe ndi mmodzi yemwe amene adzadutsemo.
Mʼdzikomo mudzakhala akabawi ndi anungu;
amantchichi ndi akhwangwala adzapanga zisa zawo mʼmenemo.
Mulungu adzatambalitsa pa Edomu
chingwe choyezera cha chisokonezo
ndi chingwe chowongolera cha chiwonongeko.
Anthu olemekezeka ake sadzatchedwanso mfumu kumeneko;
akalonga ake onse adzachotsedwa.
Minga idzamera mʼnyumba zake zankhondo zotetezedwa,
khwisa ndi mitungwi zidzamera mʼmalinga ake.
Ankhandwe azidzadya mʼmenemo;
malo okhalamo akadzidzi.
Avumbwe adzakumana ndi afisi,
ndipo zirombo za mʼchipululu zizidzayitanizana.
Kumeneko kudzafikanso mizimu yoyipa
ndi kupeza malo opumulirako.
Kadzidzi adzamangako chisa chake nʼkuyikirako mazira,
adzaswa ana ake ndi kusamalira ana ake mu mthunzi wa mapiko ake;
akamtema adzasonkhananso kumeneko,
awiriawiri.
Funafunani mʼbuku la Yehova ndi kuwerenga:
mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasowa;
sipadzakhala nʼchimodzi chomwe chopanda chinzake.
Pakuti Yehova walamula kuti zitero,
ndipo Mzimu wake udzawasonkhanitsa pamodzi.
Yehova wagawa dziko lawo;
wapatsa chilichonse chigawo chake.
Dziko lidzakhala lawo mpaka muyaya
ndipo zidzakhala mʼmenemo pa mibado yonse.
Chimwemwe cha Opulumutsidwa
Chipululu ndi dziko lopanda madzi zidzasangalala;
dziko lowuma lidzakondwa
ndi kuchita maluwa. Dzikolo lidzakhala ndi maluwa ochuluka
lidzasangalala kwambiri ndi kufuwula mwachimwemwe.
Lidzakhala ndi ulemerero monga wa ku mapiri a ku Lebanoni,
maonekedwe ake wokongola adzakhala ngati a ku Karimeli ndi a ku Saroni.
Aliyense adzaona ulemerero wa Yehova,
ukulu wa Mulungu wathu.
Limbitsani manja ofowoka,
limbitsani mawondo agwedegwede;
nenani kwa a mitima yamantha kuti;
“Limbani mtima, musachite mantha;
Mulungu wanu akubwera,
akubwera kudzalipsira;
ndi kudzabwezera chilango adani anu;
akubwera kudzakupulumutsani.”
Pamenepo maso a anthu osaona adzapenyanso
ndipo makutu a anthu osamva adzatsekuka.
Anthu olumala adzalumpha ngati mbawala,
ndipo osayankhula adzayimba mokondwera.
Akasupe adzatumphuka mʼchipululu
ndipo mitsinje idzayenda mʼdziko lowuma,
mchenga wotentha udzasanduka dziwe,
nthaka yowuma idzasanduka ya akasupe.
Pamene panali mbuto ya ankhandwe
padzamera udzu ndi bango.
Ndipo kumeneko kudzakhala msewu waukulu;
ndipo udzatchedwa Msewu Wopatulika.
Anthu odetsedwa
sadzayendamo mʼmenemo;
zitsiru sizidzasochera mʼmenemo.
Kumeneko sikudzakhala mkango,
ngakhale nyama yolusa sidzafikako;
sidzapezeka konse kumeneko.
Koma okhawo amene Yehova anawapulumutsa adzayenda mu msewu umenewu.
Iwo amene Yehova anawawombola adzabwerera.
Adzalowa mu mzinda wa Ziyoni akuyimba;
kumeneko adzakondwa mpaka muyaya.
Adzakutidwa ndi chisangalalo ndi chimwemwe,
ndipo chisoni ndi kudandaula zidzatheratu.
Senakeribu Awopseza Yerusalemu
Chaka cha khumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya ku Yuda, nayilanda. Kenaka mfumu ya ku Asiriya inatuma kazembe wake wankhondo pamodzi ndi gulu lalikulu lankhondo kuchokera ku Lakisi kupita kwa mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Tsono kazembeyo anayima pafupi ndi ngalande yamadzi yochokera ku Dziwe lakumtunda pa msewu wopita ku malo a munda wa mmisiri wochapa zovala. Panali anthu atatu. Woyamba anali Eliyakimu mwana wa Hilikiya komanso ndiye woyangʼanira nyumba ya mfumu. Wachiwiri anali Sebina amene anali mlembi wa bwalo; ndipo wachitatu anali Yowa mwana wa Asafu komanso anali wolemba zochitika. Anthu awa anatuluka kukakumana ndi kazembe wa ankhondo uja.
Kazembe wa ankhondo anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,
“Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani? Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira. Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, ‘Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake, Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, ‘Muzipembedza pa guwa lansembe ili?’
“Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: Ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! Iwe ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo. Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.”
Pamenepo Eliyakimu, Sebina ndi Yowa anawuza kazembeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
Koma kazembeyo anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
Tsono kazembeyo anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! Zimene mfumu ikunena ndi izi: Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni! Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
“Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, mpaka mfumuyo itabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanulo, dziko limene lili ndi tirigu ndi vinyo watsopano, dziko loyenda mkaka ndi uchi.
“Inu musalole kuti Hezekiya akusocheretseni pamene iye akuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi alipo mulungu wa anthu a mtundu wina amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”
Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu; Sebina mlembi wa bwalo; ndi Yowa, mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza zonse zimene anayankhula kazembe uja.
Hezekiya Apempha Thandizo kwa Yehova
Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. Iye anatuma Eliyakimu woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo, ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera.’ Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a kazembe amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.”
Akuluakulu a mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake, ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
Kazembe wa ankhondo uja atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi akubwera kudzachita naye nkhondo. Atamva zimenezi, anatumiza amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya ku Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ Ndithudi iwe unamva zimene mafumu a ku Asiriya akhala akuchitira mayiko onse. Iwo anawawononga kotheratu. Tsono iwe ndiye ndi kupulumuka? Makolo anga anawononga mizinda ya Gozani, Harani, Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene ankakhala ku Telasara. Kodi milungu inayi ija anawapulumutsa anthu a mizindayi? Kodi mafumu a ku Hamati, Aripadi, Safaravaimu, Hena ndi Iva ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
Hezekiya analandira kalata kwa amithenga nayiwerenga pomwepo. Hezekiya anapita ku Nyumba ya Yehova ndipo anayika kalatayo pamaso pa Yehova. Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova: “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, amene mumakhala pa mpando wanu waufumu pakati pa akerubi, Inu nokha ndiye Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Inu Yehova tcherani khutu ndipo mumve. Inu Yehova, tsekulani maso anu ndipo muone. Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza, kunyoza Mulungu wamoyo.
“Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu yonse ya anthu ndi mayiko awo. Iwo anaponyera pa moto milungu yawo ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mafano a mitengo ndi miyala, yopangidwa ndi manja a anthu. Tsono Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼdzanja lake kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndiye Mulungu.”
Yehova Ayankha Pemphero la Hezekiya
Tsono Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga wochokera kwa Yehova kwa Hezekiya poyankha pemphero lake lokhudza Senakeribu mfumu ya ku Asiriya. Mawu amene Yehova wayankhula motsutsana naye ndi awa:
“Mwana wamkazi wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu,
akupukusa mutu wake pamene iwe ukuthawa.
Kodi iwe wanyoza ndi kulalatira ndani?
Kodi iwe wafuwulira
ndi kumuyangʼana monyada ndani?
Watsutsana ndi Woyerayo wa Israeli!
Kudzera mwa amithenga ako
iwe wanyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta anga ochuluka
ndafika pamwamba pa mapiri,
pamwamba penipeni pa mapiri a Lebanoni.
Ndagwetsa mitengo yamkungudza yayitali kwambiri,
ndi mitengo yabwino kwambiri ya payini.
Ndafika pa msonga pake penipeni,
nkhalango yake yowirira kwambiri.
Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndi kumva madzi akumeneko
ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’
“Kodi sunamvepo
kuti zimenezi ndinazikonzeratu kalekale?
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndazichitadi,
kuti iwe kwako nʼkusandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
Anthu amene ankakhala kumeneko analibenso mphamvu,
ankada nkhawa ndi kuchititsidwa manyazi.
Anali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu omera pa denga,
umene mphepo imawumitsa usanakule nʼkomwe.
“Koma Ine ndimadziwa zonse za iwe;
ndimadziwa pamene ukuyima ndi pamene ukukhala; ndimadziwa pamene ukutuluka ndi pamene ukulowa,
ndiponso momwe umandikwiyira Ine.
Chifukwa umandikwiyira Ine
ndi kuti mwano wako wamveka mʼmakutu anga,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndikuyika chitsulo mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokuyendetsa
njira yomwe unadzera pobwera.
“Iwe Hezekiya, chizindikiro chako cha zimene zidzachitike ndi ichi:
“Chaka chino mudzadya zimene zamera zokha,
ndipo chaka chachiwiri zimene zaphukira pa zomera zokha,
koma chaka chachitatu mudzafesa ndi kukolola,
mudzawoka mitengo yamphesa ndi kudya zipatso zake.
Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsalire
adzazika mizu yawo pansi ndipo adzabereka zipatso poyera.
Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni gulu la anthu opulumuka.
Changu cha Yehova Wamphamvuzonse
chidzachita zimenezi.
“Choncho Yehova akunena izi za mfumu ya ku Asiriya:
“Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi uliwonse.
Sadzafika pafupi ndi mzindawu ndi ankhondo ake a zishango
kapena kuwuzinga ndi mitumbira yankhondo.
Adzabwerera potsata njira yomwe anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,”
akutero Yehova.
“Ine ndidzawuteteza ndi kuwupulumutsa mzindawu,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha pangano ndi mtumiki wanga Davide!”
Tsopano mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya nkhondo ya ku Asiriya ndikukapha asilikali 185,000. Podzuka mmawa mwake anthu anangoona mitembo ponseponse! Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anasasula misasa nʼkuchoka kubwerera kukakhala ku Ninive.
Tsiku lina, pamene ankapembedza mʼnyumba ya mulungu wake, Nisiroki, ana ake awiri, Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga, ndipo anathawira mʼdziko la Ararati. Ndipo mwana wake Esrahadoni analowa ufumu mʼmalo mwake.
Kudwala kwa Hezekiya
Nthawi imeneyo Mfumu Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anati “Yehova akuti: Konza bwino nyumba yako, pakuti ukufa; suchira.”
Hezekiya anatembenuka nayangʼana kukhoma, napemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kumbukirani momwe ndayendera pamaso panu mokhulupirika ndi modzipereka ndipo ndakhala ndikuchita zabwino pamaso panu.” Ndipo Hezekiya analira mosweka mtima.
Ndipo Yehova analamula Yesaya kuti: “Pita kwa Hezekiya ndipo ukamuwuze kuti, ‘Yehova, Mulungu wa kholo lake Davide akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona; ndidzakuwonjezera zaka 15 pa moyo wako. Ndipo ndidzakupulumutsa, iwe pamodzi ndi mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya, Ine ndidzawuteteza mzindawu.
“ ‘Ichi ndi chizindikiro cha Yehova kwa iwe kutsimikiza kuti Yehova adzachita zimene walonjeza: Chithunzithunzi chimene dzuwa likuchititsa pa makwerero a Ahazi ndidzachibweza mʼmbuyo makwerero khumi.’ ” Ndipo chithunzithunzi chinabwerera mʼmbuyo makwerero khumi.
Ndakatulo ya Hezekiya mfumu ya ku Yuda imene analemba atadwala ndi kuchira:
Ine ndinaganiza kuti
ndidzapita ku dziko la akufa
pamene moyo ukukoma.
Ndinaganiza kuti, “Sindidzaonanso Yehova,
mʼdziko la anthu amoyo,
sindidzaonanso mtundu wa anthu
kapena kukhala pamodzi ndi amene amakhala pa dziko lapansi lino.
Nyumba yanga yasasuka
ndipo yachotsedwa.
Ngati tenti ya mʼbusa mwapindapinda moyo wanga,
ngati munthu wowomba nsalu;
kuyambira usana mpaka usiku mwakhala mukundisiya.
Ndinkalira kupempha chithandizo usiku wonse mpaka mmawa;
koma Inu Yehova munaphwanya mafupa anga ngati mkango,
ndipo mwakhala mukundisiya.
Ndinkalira ngati namzeze kapena chumba,
ndinkabuwula ngati nkhunda yodandaula.
Maso anga anatopa nʼkuyangʼana mlengalenga.
Inu Ambuye, ine ndili mʼmavuto bwerani mudzandithandize!”
Koma ine ndinganene chiyani?
Yehova wayankhula nane, ndipo Iye ndiye wachita zimenezi.
Chifukwa cha kuwawa kwa mtima wanga,
ine ndidzayenda modzichepetsa masiku amoyo wanga onse.
Ambuye, masiku anga ali mʼmanja mwanu.
Mzimu wanga upeza moyo mwa Inu.
Munandichiritsa ndi
kundikhalitsa ndi moyo.
Ndithudi, ine ndinamva zowawa zotere
kuti ndikhale ndi moyo;
Inu munandisunga
kuti ndisapite ku dzenje la chiwonongeko
chifukwa mwakhululukira
machimo anga onse.
Pakuti akumanda sangathe kukutamandani,
akufa sangayimbe nyimbo yokutamandani.
Iwo amene akutsikira ku dzenje
sangakukhulupirireni.
Amoyo, amoyo okha ndiwo amakutamandani,
monga mmene ndikuchitira ine lero lino;
abambo amawuza ana awo za
kukhulupirika kwanu.
Yehova watipulumutsa.
Tiyeni tiyimbe ndi zoyimbira za zingwe
masiku onse a moyo wathu
mʼNyumba ya Yehova.
Yesaya anati, “Anthu atenge mʼbulu wankhunyu ndipo apake pa chithupsacho ndipo Hezekiya adzachira.”
Hezekiya nʼkuti atafunsa kuti, “Kodi chizindikiro chako nʼchiyani chotsimikiza kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova?”
Nthumwi Zochokera ku Babuloni
Nthawi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani mfumu ya ku Babuloni anatumiza nthumwi kwa Hezekiya nawapatsira makalata ndi mphatso, pakuti anamva za kudwala kwake ndi kuti anachira. Hezekiya anawalandira mwasangala ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo siliva, golide, zokometsera zakudya, mafuta abwino kwambiri, zida zonse zankhondo ndiponso zonse zimene zinkapezeka mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse ka mʼnyumba yaufumu kapena mu ufumu wake onse kamene sanawaonetse.
Tsono mneneri Yesaya anapita kwa mfumu Hezekiya ndipo anamufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani chiyani, ndipo anachokera kuti?”
Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
Mneneri anafunsanso kuti, “Kodi mʼnyumba yanu yaufumu anaonamo chiyani?”
Hezekiya anati, “Anaona chilichonse cha mʼnyumba yanga yaufumu. Palibe ndi chimodzi chomwe za mʼnyumba yosungiramo chuma changa chimene sindinawaonetse.”
Pamenepo Yesaya anati kwa Hezekiya, “Imvani mawu a Yehova Wamphamvuzonse: Yehova akuti, nthawi idzafika ndithu pamene zonse za mʼnyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu anazisonkhanitsa mpaka lero lino, zidzatengedwa kupita nazo ku Babuloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe. Ndipo ena mwa ana anu, obala inu amene adzatengedwanso, ndipo adzawasandutsa adindo ofulidwa mʼnyumba ya mfumu ya ku Babuloni.”
Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhula ndi abwino.” Ponena izi iye ankaganiza kuti, “Padzakhala mtendere ndi chitetezo masiku a moyo wanga onse.”
Mawu a Chitonthozo kwa Anthu a Mulungu
Atonthozeni, atonthozeni anthu anga,
akutero Mulungu wanu.
Ayankhuleni moleza mtima anthu a ku Yerusalemu
ndipo muwawuzitse
kuti nthawi ya ukapolo wawo yatha,
tchimo lawo lakhululukidwa.
Ndawalanga mokwanira
chifukwa cha machimo awo onse.
Mawu a wofuwula mʼchipululu akuti,
“Konzani njira ya Yehova
mʼchipululu;
wongolani njira zake;
msewu owongoka wa Mulungu wathu mʼdziko lopanda kanthu.
Chigwa chilichonse achidzaze.
Phiri lililonse ndi chitunda chilichonse azitsitse;
Dziko lokumbikakumbika alisalaze,
malo azitundazitunda awasandutse zidikha.
Ndipo ulemerero wa Yehova udzaonekera,
ndipo mitundu yonse ya anthu idzawuona,
pakuti wanena zimenezi ndi Yehova.”
Wina ananena kuti, “Lengeza.”
Ndipo ine ndinati, “Kodi ndifuwule chiyani?
“Pakuti anthu onse ali ngati udzu
ndipo kukongola kwawo kuli ngati maluwa akuthengo.
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota
chifukwa cha kuwomba kwa mpweya wa Yehova.”
Mawu aja anatinso, “Ndithudi anthu sasiyana ndi udzu.
Udzu umanyala ndipo maluwa amafota,
koma mawu a Mulungu wathu adzakhalapo mpaka muyaya.”
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Ziyoni,
kwera pa phiri lalitali.
Iwe amene ukulengeza nkhani yabwino ku Yerusalemu,
fuwula kwambiri,
kweza mawu, usachite mantha;
uza mizinda ya ku Yuda kuti,
“Mulungu wanu akubwera!”
Taonani, Ambuye Yehova akubwera mwamphamvu,
ndipo dzanja lake likulamulira,
taonani akubwera ndi mphotho yake
watsogoza zofunkha zako za ku nkhondo.
Iye adzasamalira nkhosa zake ngati mʼbusa:
Iye adzasonkhanitsa ana ankhosa aakazi mʼmanja mwake
ndipo Iye akuwanyamula pachifuwa chake
ndi kutsogolera bwinobwino nkhosa zoyamwitsa.
Kodi ndani akhoza kuyeza kuchuluka kwa madzi a mʼnyanja ndi chikhatho chake,
kapena kuyeza kutalika kwa mlengalenga ndi dzanja lake?
Ndani akhoza kuyeza dothi lonse la dziko lapansi mʼdengu,
kapena kuyeza kulemera kwa
mapiri ndi zitunda ndi pasikelo?
Ndani anapereka malangizo kwa Mzimu wa Yehova
kapena kumuphunzitsa Iye monga phungu wake?
Kodi Yehova anapemphapo nzeru kwa yani kuti akhale wopenya,
kapena kuti aphunzire njira yoyenera ndi nzeru?
Iye anapempha nzeru kwa yani
ndi njira ya kumvetsa zinthu?
Ndithudi mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi ochoka mu mtsuko.
Iwo akungoyesedwa ngati fumbi chabe pa sikelo;
mʼmanja mwa Yehova zilumba nʼzopepuka ngati fumbi.
Nkhalango ya ku Lebanoni singakwanire nkhuni zosonkhera moto pa guwa lansembe,
ngakhale nyama zake sizingakwanire kupereka nsembe zopsereza.
Pamaso pa Yehova mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chopandapake;
Iye amayiwerengera ngati chinthu chopanda phindu
ndi cha chabechabe.
Kodi tsono Mulungu mungamuyerekeze ndi yani?
Kodi mungamufanizire ndi chiyani?
Likakhala fano, mʼmisiri ndiye analipanga
ndipo mʼmisiri wa golide amalikuta ndi golide
naliveka mkanda wasiliva.
Mʼmphawi amene sangathe kupeza ngakhale chopereka nsembe chotere
amasankha mtengo umene sudzawola,
nafunafuna mʼmisiri waluso woti
amupangire fano limene silingasunthike.
Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Kodi sanakuwuzeni kuyambira pachiyambi pomwe?
Kodi simunamvetsetse chiyambire cha dziko lapansi?
Yehova amene amakhala pa mpando wake waufumu kumwamba ndiye analenga dziko lapansi,
Iye amaona anthu a dziko lapansi ngati ziwala.
Ndipo anafunyulula mlengalenga ngati nsalu yotchinga,
nayikunga ngati tenti yokhalamo.
Amatsitsa pansi mafumu amphamvu
nasandutsa olamula a dziko kukhala achabechabe.
Inde, iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene
kapena kufesedwa chapompano,
ndi kungoyamba kuzika mizu kumene
ndi pamene mphepo imawombapo nʼkuziwumitsa
ndipo kamvuluvulu amaziwulutsa ngati mankhusu.
Woyera uja akuti, “Kodi mudzandiyerekeza Ine ndi yani?
Kapena kodi alipo wofanana nane?”
Tayangʼanani mlengalenga ndipo onani.
Kodi ndani analenga zonsezi mukuzionazi?
Yehova ndiye amene amazitsogolera ngati gulu la ankhondo,
nayitana iliyonse ndi dzina lake.
Ndipo popeza Iye ali ndi nyonga zambiri,
palibe ndi imodzi yomwe imene inasowapo.
Iwe Yakobo, chifukwa chiyani umanena
ndi kumadandaula iwe Israeli, kuti,
“Yehova sakudziwa mavuto anga,
Mulungu wanga sakusamala zomwe zikundichitikira ine?”
Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Yehova ndiye Mulungu wamuyaya,
ndiyenso Mlengi wa dziko lonse lapansi.
Iye sadzatopa kapena kufowoka
ndipo palibe amene angadziwe maganizo ake.
Iye amalimbitsa ofowoka
ndipo otopa amawawonjezera mphamvu.
Ngakhale achinyamata amalefuka ndi kufowoka,
ndipo achinyamata amapunthwa ndi kugwa;
koma iwo amene amakhulupirira Yehova
adzalandira mphamvu zatsopano.
Adzawuluka ngati chiwombankhanga;
adzathamanga koma sadzalefuka,
adzayenda koma sadzatopa konse.
Mulungu Thandizo la Israeli
“Khalani chete pamaso panga, inu mayiko a mʼmbali mwa nyanja!
Alekeni ayandikire ndi kuyankhula;
tiyeni tikhale pamodzi
kuti atiweruze.
“Ndani anadzutsa wochokera kummawa
uja amene ananka napambana kulikonse kumene ankapita?
Iye amapereka anthu a mitundu ina mʼmanja mwake
ndipo ndi lupanga lake anagonjetsa
ndi kusandutsa mafumu kukhala ngati fumbi
nawamwaza ngati mankhusu ndi uta wake.
Amawalondola namayenda mosavutika,
mʼnjira imene mapazi ake sanayendemo kale.
Ndani anachita zimenezi ndi kuzitsiriza,
si uja amene anayambitsa mitundu ya anthu?
Ine Yehova, ndine chiyambi
ndipo potsiriza pake ndidzakhalapo.”
Mayiko amʼmbali mwa nyanja aona zimenezi ndipo akuopa;
anthu a ku mathero a dziko lapansi akunjenjemera.
Akuyandikira pafupi, akubwera;
aliyense akuthandiza mnzake
ndipo akuwuza mʼbale wake kuti, “Limba mtima!”
Mʼmisiri wa matabwa amalimbikitsa mʼmisiri wa golide,
ndipo iye amene amasalaza fano ndi nyundo
amalimbikitsa amene amalisanja pa chipala.
Ponena za kuwotcherera iye amati, “Zili bwino.”
Iye amalikhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
“Koma Iwe Israeli mtumiki wanga,
Yakobo amene ndakusankha,
Ndiwe chidzukulu cha Abrahamu bwenzi langa.
Ndinakutengani kuchokera ku mapeto a dziko lapansi,
ndinakuyitanani kuchokera ku mbali za kutali za dziko lapansi.
Ine ndinati, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga;’
Ndinakusankha ndipo sindinakutaye.
Tsono usaope, pakuti Ine ndili nawe;
usataye mtima chifukwa Ine ndine Mulungu wako.
Ndidzakupatsa mphamvu ndipo ndidzakuthandiza,
ndidzakutchinjiriza ndi dzanja langa lamanja logonjetsa.
“Onse amene akupsera mtima
adzachita manyazi ndithu ndi kunyazitsidwa;
onse amene akukangana nawe
sadzakhalanso kanthu, adzawonongeka.
Udzafunafuna adani ako,
koma sadzapezeka.
Iwo amene akuchita nawe nkhondo
sadzakhalanso kanthu.
Pakuti Ine Yehova, ndine Mulungu wako,
amene ndikukugwira dzanja lako lamanja
ndipo ndikuti, usaope;
ndidzakuthandiza.
Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,
iwe wochepa mphamvu Israeli,
chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”
akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
“Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu
chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.
Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,
ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso
adzamwazika ndi kamvuluvulu.
Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,
ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
“Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,
koma sakuwapeza;
ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.
Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;
Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,
ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.
Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi
ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
Mʼchipululu ndidzameretsa
mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.
Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo
ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
kuti anthu aone ndi kudziwa;
inde, alingalire ndi kumvetsa,
kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;
kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
“Yehova akuwuza milungu ina kuti, ‘Fotokozani mlandu wanu.’
Mfumu ya Yakobo ikuti, ‘Perekani umboni wanu.’
Bwerani ndi milungu yanu kuti idzatiwuze
zomwe zidzachitike mʼtsogolo.
Tifotokozereni zinthu zamakedzana
tiziganizire
ndi kudziwa zotsatira zake.
Kapena tiwuzeni zimene zidzachitike mʼtsogolo,
tiwuzeni kuti kutsogolo kuli zotani,
ndipo ife tidziwa kuti ndinu milungu.
Chitani chinthu chabwino kapena choyipa,
ndipo mutidabwitsa ndi kutichititsa mantha.
Koma inu sindinu kanthu
ndipo zochita zanu nʼzopandapake;
amene amapembedza inu ali ngati chinthu chokanidwa chifukwa ndi choyipa.
“Ndinawutsa munthu wina kumpoto ndipo anabwera,
munthu wochokera kummawa amene ndinamuyitana.
Amapondaponda olamulira ngati matope,
ngati ndi wowumba mbiya amene akuponda dongo.
Ndani anawululiratu zimenezi poyamba pomwe, kuti ife tidziwe,
kapena kutiwuziratu zisanachitike kuti ife tinene kuti, ‘Analondola?’
Palibe amene ananena,
palibe analengeza zimenezi,
palibe anamva mawu anu.
Ine ndinali woyamba kumuwuza Ziyoni kuti, ‘Taona, si awa akubwera apawa!’
Ndinatumiza mthenga wa nkhani yabwino ku Yerusalemu.
Koma ndikayangʼana palibe ndi mmodzi yemwe,
palibe ndi mmodzi yemwe pakati pawo wotha kupereka uphungu,
palibe woti ayankhe pamene ine ndawafunsa.
Taonani, milungu yonseyi ndi yachinyengo!
Zochita zawo si kanthu konse;
mafano awo ali ngati mphepo yachabechabe.
Mtumiki wa Yehova
“Nayu mtumiki wanga, amene ndimamuchirikiza,
amene ndamusankha, amenenso ndimakondwera naye.
Ndayika Mzimu wanga mwa Iyeyo,
ndipo adzaweruza anthu a mitundu yonse mwachilungamo.
Iye sadzafuwula, sadzamveka mawu,
kapena mawu ake kumveka mʼmisewu.
Bango lophwanyika sadzalithyola,
ndipo moto wozilala sadzawuzimitsa.
Motero adzaonetsa kuti chilungamo ndicho choonadi;
sadzafowoka kapena kukhumudwa
mpaka atakhazikitsa chilungamo pa dziko lapansi,
ndi mpaka mayiko a mʼmbali mwa nyanja atafika poyembekezera malangizo ake.”
Yehova Mulungu
amene analenga zamlengalenga ndi kuziyalika,
amene analenga dziko lapansi ndi zonse zimene zimabereka,
amenenso amapereka mpweya kwa anthu ake okhala mʼdzikomo,
ndi moyo kwa onse oyendamo, akuti,
“Ine Yehova, ndakuyitana chifukwa Ine ndine wolungama;
ndikugwira dzanja ndipo
ndidzakuteteza.
Ndakupereka kukhala pangano langa kwa anthu
ndi kuwunika kwa anthu a mitundu ina.
Udzatsekula maso a anthu osaona,
udzamasula anthu a mʼndende
ndi kutulutsa mʼndende anthu okhala mu mdima.
“Ine ndine Yehova: dzina langa ndi limenelo!
Sindidzapereka ulemerero wanga kwa wina aliyense
kapena matamando anga kwa mafano.
Taonani, zinthu zimene ndinalosera kale zachitikadi,
ndipo ndikuwuzani zinthu zatsopano;
zinthuzo zisanaonekere
Ine ndakudziwitsani.”
Nyimbo Yotamanda Yehova
Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,
mutamandeni inu okhala mʼdziko lonse lapansi,
inu amene mumayenda pa nyanja, nyanja ikokome ndi zonse zili mʼmenemo.
Inu okhala pa zilumba tamandani Yehova.
Chipululu ndi mizinda yake zikweze mawu awo;
midzi ya Akedara ikondwere.
Anthu a ku Sela ayimbe mwachimwemwe;
afuwule kuchokera pamwamba pa mapiri.
Atamande Yehova
ndipo alalike matamando ake kwa anthu apazilumba zonse.
Yehova adzapita ku nkhondo ngati munthu wamphamvu,
adzawutsa ukali wake ngati munthu wankhondo;
akukuwa ndiponso akufuwula mfuwu wankhondo
ndipo adzagonjetsa adani ake.
Yehova akuti, “Ndakhala ndili chete kwa nthawi yayitali,
ndakhala ndili phee osachita kanthu.
Koma tsopano, ngati mayi pa nthawi yochira,
ndi kubuwula ndi kupuma modukizadukiza ndipo ndili wefuwefu.
Ndidzawononga mapiri ndi zitunda
ndipo ndidzawumitsa zomera zawo zonse;
ndidzasandutsa mitsinje kukhala zilumba
ndipo ndidzawumitsa maiwe.
Ndidzatsogolera anthu osaona mʼmisewu imene sanayidziwe,
ndidzawatsogolera mʼnjira zimene sanayendepo;
ndidzasandutsa mdima wa kutsogolo kwawo kuti ukhale kuwala
ndipo ndidzasalaza malo osalala.
Zimenezi ndizo ndidzachite;
sindidzawataya.
Koma onse amene amadalira mafano
amene amanena kwa mafanowo kuti, ‘ndinu milungu yathu,’
ndidzawachititsa manyazi kotheratu.
Aisraeli Alephera Kuphunzira
“Imvani, agonthi inu;
yangʼanani osaona inu, kuti muone! Ali wosaona ndani, si mtumiki wanga kodi?
Ndipo ndani ali wosamva ngati mthenga amene ndamutuma?
Kodi ndani ali wosaona ngati uja ndinachita naye pangano,
kapena wosaona ndani ngati mtumiki wa Yehova?
Iwe waona zinthu zambiri, koma sunazisamale;
makutu ako ndi otsekuka koma sumva kanthu.”
Chinamukomera Yehova
chifukwa cha chilungamo chake,
kapena lamulo lake kukhala lalikulu ndi lopambana.
Koma awa ndi anthu amene afunkhidwa ndi kuwalanda zinthu zawo,
onsewa anawakola mʼmaenje
kapena akuwabisa mʼndende.
Tsono asanduka chofunkha
popanda wina wowapulumutsa
kapena kunena kuti,
“Abwezeni kwawo.”
Kodi ndani wa inu amene adzamvetsera zimenezi
kapena kutchera khutu ndi kumva za mʼtsogolomo?
Ndani anapereka Yakobo kwa ofunkha,
ndi Israeli kwa anthu akuba?
Kodi si Yehova,
amene ife tamuchimwirayu?
Pakuti sanathe kutsatira njira zake;
ndipo sanamvere malangizo ake.
Motero anawakwiyira kwambiri,
nawavutitsa ndi nkhondo.
Anayatsa moto ponseponse mowazungulira komabe iwo sanamvetse;
motowo unawapsereza, koma iwo sanatengepo phunziro ayi.
Yehova Yekha Mpulumutsi wa Israeli
Koma tsopano, Yehova
amene anakulenga, iwe Yakobo,
amene anakuwumba, iwe Israeli akuti,
“Usaope, pakuti ndakuwombola;
Ndinakuyitanitsa mokutchula dzina lako, ndiwe wanga.
Pamene ukuwoloka nyanja,
ndidzakhala nawe;
ndipo pamene ukuwoloka mitsinje,
sidzakukokolola.
Pamene ukudutsa pa moto,
sudzapsa;
lawi la moto silidzakutentha.
Chifukwa Ine Yehova, Mulungu wako,
Woyera wa Israeli, ndine Mpulumutsi wako.
Ndinapereka Igupto pofuna kuti ndiwombole iwe,
ndinapereka Kusi ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
Popeza kuti ndiwe wamtengowapatali wolemekezeka ndi wapamtima panga,
ndipo chifukwa ndimakukonda,
ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe,
ndidzapereka mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.
Usachite mantha, pakuti Ine ndili nawe;
ndidzabweretsa ana ako kuchokera kummawa,
ndipo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kumadzulo.
Ndidzawuza a kumpoto kuti, ‘Amasuleni,’
ndidzawuza akummwera kuti, ‘Musawagwire.’
Bweretsani ana anga aamuna kuchokera ku mayiko akutali,
ana anga a akazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi;
onsewo amadziwika ndi dzina langa;
ndinawalenga chifukwa cha ulemerero wanga,
ndinawawumba, inde ndinawapanga.”
Tulutsa anthu amene ali nawo maso koma sakupenya,
anthu amene ali nawo makutu koma sakumva.
Mitundu yonse ya anthu isonkhane pamodzi,
anthu a mitundu ina akhale pamodzi pabwalo la milandu.
Ndani wa iwo amene ananeneratu zimenezi?
Ndani wa iwo anatifotokozerapo zinthu zakalekale?
Abweretu ndi mboni zawo kuti adzatsimikizire kuti ananena zoona,
kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, “Ndi zoona.”
Yehova akunena kuti, “Inu Aisraeli ndinu mboni zanga,
ndi mtumiki wanga amene ndinakusankha,
kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, ndipo mudzamvetsa kuti Mulungu ndine ndekha.
Patsogolo panga sipanapangidwepo mulungu wina,
ngakhale pambuyo panga
sipadzakhalaponso wina.”
Akutero Yehova, “Ine, Inetu ndine Yehova,
ndipo palibe Mpulumutsi wina koma Ine ndekha.
Ndine amene ndinaneneratu, amene ndinakupulumutsa;
ndine, osati mulungu wina wachilendo pakati panu amene ndinalengezeratu.
Inu ndinu mboni zanga, kuti Ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.
“Ine ndine Mulungu kuyambira nthawi yamakedzana, ndipo ndidzakhalabe Mulungu ku nthawi zonse.
Palibe amene angathe kuthawa mʼmanja mwanga,
ndipo chimene ndachita palibe angathe kuchisintha.”
Chifundo cha Mulungu ndi Kusakhulupirika kwa Israeli
Yehova akuti,
Mpulumutsi wanu, Woyerayo wa Israeli akuti,
“Chifukwa cha inu ndidzatuma gulu lankhondo kukalimbana ndi Babuloni
ndi kukupulumutsani.
Ndidzagwetsa zitseko zonse za mzindawo, ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.
Ine ndine Yehova, Woyera wanu uja,
Mlengi wa Israeli. Ine ndine Mfumu yanu.”
Yehova
anapanga njira pa nyanja,
anapanga njira pakati pa madzi amphamvu.
Iye anasonkhanitsa magaleta, akavalo,
gulu lankhondo ndi asilikali amphamvu,
ndipo onse anagwa pamenepo, osadzukanso
anazimitsidwa kutheratu ngati chingwe cha nyale. Yehova ameneyu akuti,
“Iwalani zinthu zakale;
ndipo musaganizirenso zinthu zimene zinachitika kale.
Taonani, Ine ndikuchita zinthu zatsopano!
Tsopano zayamba kale kuoneka; kodi simukuziona?
Ine ndikulambula msewu mʼchipululu
ndi kupanga mitsinje mʼdziko lowuma.
Nyama zakuthengo, nkhandwe ndi akadzidzi
zinandilemekeza.
Ndidzayendetsa mitsinje mʼdziko lowuma
kuti ndiwapatse madzi anthu anga
osankhidwa.
Anthu amene ndinadziwumbira ndekha
kuti aziyimba nyimbo yotamanda Ine.
“Komatu simunapemphera kwa Ine, Inu a mʼbanja la Yakobo,
munatopa nane, Inu Aisraeli.
Simunabweretse kwa Ine nkhosa za nsembe zopsereza,
kapena kundilemekeza ndi nsembe zanu.
Ine sindinakulemetseni pomakupemphani zopereka za chakudya
kapena kukutopetsani pomakupemphani nsembe zofukiza.
Simunandigulire bango lonunkhira
kapena kundipatsa Ine mafuta okwanira a nsembe zanu.
Koma inu mwandilemetsa Ine ndi machimo anu
ndipo mwanditopetsa Ine ndi zolakwa zanu.
“Ine, Inetu, ndi amene ndimafafaniza
zolakwa zanu, chifukwa cha Ine mwini,
ndipo sindidzakumbukiranso machimo anu.
Mundikumbutse zakale,
ndipo titsutsane nkhaniyi pamodzi;
fotokozani mlandu wanu kuti muonetse kuti ndinu osalakwa.
Kholo lanu loyamba linachimwa;
ndipo Atsogoleri anu achipembedzo anandiwukira.
Chifukwa chake Ine ndidzanyazitsa akuluakulu a Nyumba yanu ya mapemphero,
ndipo ndidzapereka Yakobo kuti awonongedwe
ndi Israeli kuti achitidwe chipongwe.”
Israeli Wosankhidwa wa Yehova
Yehova akuti, “Mvera tsopano, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
Israeli, amene ndinakusankha.
Yehova
amene anakupanga iwe, anakuwumba iwe mʼmimba ya amayi ako,
ndi amene adzakuthandiza iwe. Iye akuti,
Usachite mantha, iwe Yakobo, mtumiki wanga,
Yesuruni, amene ndinakusankha.
Pakuti ndidzathira madzi pa nthaka yowuma,
ndi kuyendetsa mitsinje mʼdziko lowuma;
ndidzatumiza Mzimu wanga pa ana anu,
ndi kutsitsa madalitso anga pa zidzukulu zanu.
Iwo adzakula ngati udzu wothirira bwino
ndi ngati bango lomera mʼmbali mwa mitsinje ya madzi oyenda.
Wina adzanena kuti, ‘Ine ndine wa Yehova;’
wina adzadzitcha yekha wa banja la Yakobo;
winanso adzalemba pa dzanja lake, ‘Wa Yehova’
ndipo adzadzitcha wa banja la Israeli.
Yehova, Osati Mafano
“Yehova Mfumu
ndi Mpulumutsi wa Israeli, Yehova Wamphamvuzonse akuti:
Ine ndine woyamba ndi wotsiriza;
palibenso Mulungu wina koma Ine ndekha.
Ndani nanga angafanane ndi Ine? Muloleni kuti ayankhule.
Muloleni andifotokozere ndi kundiyalira bwino lomwe
zimene zinachitika kuyambira pamene ndinkakhazikitsa anthu anga akalekale,
ndi ziti zimene zidzachitike;
inde, muloleni alosere zimene zikubwera.
Musanjenjemere, musachite mantha.
Kodi sindinakuwuzeni zimenezi ndi kuzilosera kalekale lomwe?
Inu ndinu mboni zanga. Kodi aliponso Mulungu wina kupatula Ine?
Ayi, palibe Thanthwe linanso limene sindikulidziwa.”
Onse amene amapanga mafano ngachabe,
ndipo milungu imene amayilemekeza ndi yopanda phindu.
Iwo amene amapembedza mafano ndi wosaona;
ndipo sazindikira kanthu. Choncho adzawachititsa manyazi.
Ndani amasema mulungu ndi kuwumba fano,
limene silingamupindulire?
Iye pamodzi ndi anzake onse adzawachititsa manyazi;
amisiri a mafano ndi anthu chabe.
Aloleni onse asonkhane ndi kuyima pabwalo la milandu;
onse adzaopsedwa ndipo adzachita manyazi.
Mmisiri wa zitsulo amatenga chitsulo
ndipo amachiyika pa makala amoto;
ndi dzanja lake lamphamvu
amachisula pochimenya ndi nyundo.
Pambuyo pake mʼmisiri uja amamva njala natha mphamvu;
iye samwa madzi, ndipo amalefuka.
Mmisiri wa matabwa nayenso amayeza mtengo ndi chingwe
ndipo amajambula chithunzi ndi cholembera;
amasema bwinobwino ndi chipangizo chake
ndipo amachiwongola bwino ndi chida chake.
Amachipanga ngati munthu,
munthu wake wokongola
kuti aliyike mʼnyumba yake yachipembedzo.
Amagwetsa mitengo ya mkungudza,
mwinanso amatenga mtengo wa payini kapena wa thundu
nʼkudzisankhira mtengo wabwino pakati pa mitengo ya mʼnkhalango,
ndipo amadzala mtengo wa payini ndi kuwuleka kuti ukule ndi mvula.
Mitengoyo munthu amachitako nkhuni;
nthambi zina amasonkhera moto wowotha,
amakolezera moto wophikira buledi
ndi mbali ina ya mtengowo amapangira mulungu ndipo amapembedza;
iye amapanga fano ndi kumaligwadira.
Chigawo china cha mtengowo amasonkhera moto
wowotcherapo nyama imene
amadya, nakhuta.
Iye amawotha motowo ndipo amanena kuti,
“Aa! Ndikumva kutentha; pano pali moto.”
Chigawo chotsala amapanga kamulungu, fano lake limenelo;
amaligwadira ndi kulipembedza.
Amapemphera kwa fanolo ndipo amanena kuti,
“Iwe ndiwe mulungu wanga, ndipulumutse.”
Anthu otere sadziwa kanthu, samvetsa kanthu kalikonse;
maso awo ndi omatirira ndipo sangathe kuona,
ndipo mitu yawo ndi yogontha kotero sangathe kumvetsa.
Palibe amene amayima nʼkulingalira.
Palibe wanzeru kapena womvetsa zinthu bwino woti nʼkunena kuti,
chigawo china cha mtengowo ndinasonkhera moto;
pa makala ake ndinaphikira buledi,
ndinawotchapo nyama ndipo ndinadya.
Chigawo chotsalachi ndipangire chinthu chonyansachi.
Kodi ndidzagwadira mtengo?
Munthu wotere ali ngati wodya phulusa, maganizo ake opusa amusocheretsa;
motero kuti sangathe kudzipulumutsa yekha kapena kudzifunsa kuti,
“Kodi chinthu chili mʼmanja mwangachi si chabodza?”
Yehova akuti, “Iwe Yakobo, kumbukira zinthu izi
popeza kuti ndiwe mtumiki wanga, iwe Israeli.
Ine ndinakupanga iwe, ndiwe mtumiki wanga;
iwe Israeli, sindidzakuyiwala.
Ndachotsa zolakwa zako ngati mitambo,
ndi machimo ako ngati nkhungu ya mmawa.
Bwerera kwa Ine,
popeza ndakupulumutsa.”
Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga, pakuti Yehova wachita zimenezi;
fuwula, iwe dziko lapansi.
Imbani nyimbo, inu mapiri,
inu nkhalango ndi mitengo yonse,
chifukwa Yehova wawombola Yakobo,
waonetsa ulemerero wake mwa Israeli.
Anthu Adzakhalanso mu Yerusalemu
Yehova Mpulumutsi wanu, amene
anakuwumbani mʼmimba ya amayi anu akuti:
“Ine ndine Yehova,
amene anapanga zinthu zonse,
ndinatambasula ndekha zinthu zakuthambo,
ndinayala ndekha dziko lapansi.
Ndine amene ndinalepheretsa mipingo ya anthu onyenga,
ndipo ndimapusitsa owombeza mawula.
Ndimasokoneza anthu a nzeru,
ndi kuonetsa kuti nzeru zawo nʼzopusa.
Ndine amene ndimatsimikiza mawu a atumiki ake
ndi kukwaniritsa zimene analosera amithenga ake.
“Ndine amene ndinanena za Yerusalemu kuti mudzakhalanso anthu.
Ndinanenanso za mizinda ya Yuda kuti idzamangidwanso.
Za mabwinja awo ndinanena kuti ndidzawawutsanso.
Ndine amene ndinawuza nyanga yayikulu kuti, ‘Uma’
ndipo ndidzawumitsa mitsinje yako.
Ndine amene ndinanena kwa Koresi kuti, ‘Iye ndiye mʼbusa wanga,’
ndipo adzachita zonse zimene ndikufuna;
iye adzalamula kuti, ‘Yerusalemu amangidwenso’
ndi kuti, ‘Maziko a Nyumba ya Mulungu ayikidwenso.’ ”
Yehova akuyankhula ndi wodzozedwa wake
Koresi amene anamugwira dzanja lamanja
kuti agonjetse mitundu ya anthu
ndi kuwalanda mafumu zida zawo zankhondo,
ndi kutsekula zitseko
kuti zipatazo zisadzatsekedwenso ndi ichi:
Ine ndidzayenda patsogolo pako,
ndi kusalaza mapiri;
ndidzaphwanya zitseko za mkuwa
ndi kuthyola mipiringidzo ya chitsulo.
Ndidzakupatsa chuma chobisika mu mdima,
katundu wa pamalo obisika,
kotero kuti udziwe kuti Ine ndine Yehova
Mulungu wa Israeli, amene ndakuyitana pokutchula dzina.
Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo,
chifukwa cha wosankhidwa wanga Israeli,
Ine ndakuyitana pokutchula dzina
ndipo ndakupatsa dzina laulemu
ngakhale iwe sukundidziwa Ine.
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina;
kupatula Ine palibenso Mulungu wina.
Ndidzakupatsa mphamvu,
ngakhale sukundidziwa Ine,
kotero kuti kuchokera kummawa mpaka kumadzulo
anthu adzadziwa kuti palibe wina koma Ine ndekha.
Ine ndine Yehova,
ndipo palibenso wina.
Ndimalenga kuwala ndi mdima,
ndimabweretsa madalitso ndi tsoka;
ndine Yehova, amene ndimachita zonsezi.
“Iwe thambo gwetsa mvula kuchokera kumwamba;
mitambo ivumbwe mivumbi ya chilungamo.
Dziko lapansi litsekuke,
ndipo chipulumutso chiphuke kuti
chilungamo chimereponso;
Ine Yehova, ndine ndalenga zimenezi.
“Tsoka kwa wokangana ndi mlengi wake,
ngakhale kuti ali ngati phale chabe pakati pa mapale anzake.
Kodi dongo lingafunse munthu wowumba kuti,
‘Kodi ukuwumba chiyani?’
Kodi ntchito yako inganene kuti,
‘Ulibe luso?’
Tsoka kwa wofunsa abambo ake kuti,
‘Kodi munabereka chiyani?’
Kapena amayi ake kuti,
‘Kodi mufuna kubereka chiyani?’
“Yehova
Woyerayo wa Israeli, ndiponso Mlengi wake akunena,
zokhudza zinthu zimene zikubwera ndi izi:
Kodi iwe ukundifunsa za ana anga,
kapena kundilamula pa zokhudza ntchito zanga?
Ndine amene ndinapanga dziko lapansi
ndikulenga munthu kuti akhalemo.
Ine ndi manja anga ndinayalika thambo;
ndimalamulira zolengedwa zonse za mlengalenga.
Ndine amene ndidzawutsa Koresi kuti chilungamo changa chikwaniritsidwe:
ndipo ndidzawongolera njira zake zonse.
Iye adzamanganso mzinda wanga
ndi kumasula anthu anga amene ali mu ukapolo,
wopanda kupereka ndalama kapena mphotho,
akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
Yehova akuti,
“Chuma cha ku Igupto ndi chuma cha malonda cha Kusi chidzakhala chanu.
Anthu amphamvu zawo ndi athanzi a ku Seba
adzabwera kwa inu
ndipo adzakhala anthu anu;
iwo adzidzakutsatani pambuyo panu
ali mʼmaunyolo.
Adzakugwadirani
ndi kukupemphani, ponena kuti,
‘Ndithudi Mulungu ali ndi inu, ndipo palibenso wina;
palibenso mulungu wina.’ ”
Zoonadi inu muli ndi Mulungu wobisika
amene ali Mulungu ndi Mpulumutsi wa Israeli.
Onse amene amapanga mafano adzawachititsa manyazi ndi kuwanyozetsa.
Adzakhala osokonezeka maganizo.
Koma Yehova adzapulumutsa Israeli
ndi chipulumutso chamuyaya;
simudzachitanso manyazi kapena kunyozeka
mpaka kalekale.
Yehova
analenga zinthu zakumwamba,
Iye ndiye Mulungu;
amene akulenga dziko lapansi,
ndi kulikhazikitsa,
sanalipange kuti likhale lopanda kanthu,
koma analipanga kuti anthu akhalemo.
Iyeyu akunena kuti:
Ine ndine Yehova,
ndipo palibenso wina.
Ine sindinayankhule mwachinsinsi,
pamalo ena a mdima;
Ine sindinaziwuze zidzukulu za Yakobo kuti,
“Ndifunefuneni ku malo kopanda kanthu.”
Ine Yehova, ndimayankhula zoona;
ndikunena zolungama.
Yehova akuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere;
yandikirani, inu amene munapulumuka pothawa nkhondo kwa anthu a mitundu ina.
Ndinu opanda nzeru amene mumanyamula mafano a mitengo,
amene mumapemphera kwa milungu imene singathe kupulumutsa.
Fotokozani mlandu wanu,
mupatsane nzeru nonse pamodzi.
Kodi ndani ananeneratu zimenezi kalekale?
Ndani anazifotokozeratu zimenezi nthawi yamakedzana?
Kodi si Ineyo Yehova?
Ndipo palibenso Mulungu wina kupatula Ine,
Mulungu wolungama ndi Wopulumutsa,
palibenso wina kupatula Ine.
“Tembenukirani kwa Ine kuti mupulumuke,
inu anthu onse a pa dziko lapansi,
pakuti Ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
Ndalumbira ndekha,
pakamwa panga patulutsa mawu owona,
mawu amene sadzasinthika konse akuti,
bondo lililonse lidzagwada pamaso panga;
anthu onse adzalumbira potchula dzina langa.
Iwo adzanene kwa Ine kuti,
‘Chilungamo ndi mphamvu zimapezeka mwa Yehova yekha.’ ”
Onse amene anamuwukira Iye
adzabwera kwa Iye ndipo adzachita manyazi.
Koma mwa Yehova zidzukulu zonse za Israeli
zidzapambana ndi kupeza ulemerero.
Za Kupasuka kwa Babuloni ndi Mafano Ake
Beli wagwada pansi, Nebo wawerama;
nyama zonyamula katundu za nyamula milungu yawo.
Mafano awo asanduka katundu wolemera pa msana pa ngʼombe.
Asandukadi ngati katundu pa msana pa nyama zotopa.
Nyamazo zikuwerama ndi kufuna kugwa ndi milunguyo;
sizikutha kupulumutsa katunduyo,
izo zomwe zikupita ku ukapolo.
Mverani Ine, Inu nyumba ya Yakobo,
inu nonse otsala a mʼnyumba ya Israeli,
Ine ndakhala ndi kukusamalirani kuyambira mʼmimba ya amayi anu,
ndakhala ndikukunyamulani chibadwire chanu.
Mpaka pamene mudzakalambe ndi kumera imvi
ndidzakusamalirani ndithu.
Ndinakulengani ndipo ndidzakunyamulani,
ndidzakusamalirani ndi kukulanditsani.
“Kodi inu mudzandifanizira ndi yani, kapena mufananitsa ndi yani?
Kodi mudzandiyerekeza kapena kundifanizitsa ndi yani?
Anthu ena amakhuthula golide mʼzikwama zawo
ndipo amayeza siliva pa masikelo;
amalemba ntchito mʼmisiri wosula kuti awapangire mulungu,
kenaka iwo amagwada pansi ndikupembedza kamulunguko.
Amanyamula nʼkumayenda nayo milunguyo pa mapewa awo;
amayikhazika pa malo pake ndipo imakhala pomwepo.
Singathe kusuntha pamalo pakepo.
Ngakhale wina apemphere kwa milunguyo singathe kuyankha;
kapena kumupulumutsa ku mavuto ake.
“Kumbukirani zimenezi ndipo muchite manyazi,
Muzilingalire mu mtima, inu anthu owukira.
Kumbukirani zinthu zakale zinthu zamakedzana;
chifukwa Ine ndine Mulungu
ndipo palibe wina ofanana nane.
Ndinaneneratu zakumathero kuchokera pachiyambi pomwe.
Kuyambira nthawi yamakedzana ndinaloseratu zoti zidzachitike.
Ndikanena zimene ndifuna kuchita ndipo zimachitikadi.
Chilichonse chimene ndafuna ndimachichita.
Ndikuyitana chiwombankhanga kuchokera kummawa.
Ndikuyitana kuchokera ku dziko lakutali munthu amene adzakwaniritsa cholinga changa.
Zimene ndanena ndidzazikwaniritsadi;
zimene ndafuna ndidzazichitadi.
Ndimvereni, inu anthu owuma mtima,
inu amene muli kutali ndi chipulumutso.
Ndikubweretsa pafupi tsiku la chipulumutso changa;
sichili kutali.
Tsikulo layandikira
ndipo sindidzachedwa kukupulumutsani
ndi kupereka ulemerero wanga kwa Israeli.
Kugwa kwa Babuloni
“Tsika, ndi kukhala pa fumbi,
iwe namwali, Babuloni;
khala pansi wopanda mpando waufumu,
iwe namwali, Kaldeya
pakuti sadzakutchulanso wanthete kapena woyenera
kumugwira mosamala.
Tenga mphero ndipo upere ufa;
chotsa nsalu yako yophimba nkhope
kwinya chovala chako mpaka ntchafu
ndipo woloka mitsinje.
Maliseche ako adzakhala poyera
ndipo udzachita manyazi.
Ndidzabwezera chilango
ndipo palibe amene adzandiletse.”
Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wathu,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
“Khala chete, ndipo lowa mu mdima,
iwe namwali, Kaldeya;
chifukwa sadzakutchulanso
mfumukazi ya maufumu.
Ndinawakwiyira anthu anga,
osawasamalanso.
Ndinawapereka manja mwako,
ndipo iwe sunawachitire chifundo.
Iwe unachitira nkhanza
ngakhale nkhalamba.
Iwe unati, ‘Ine ndidzakhalapo nthawi zonse
ngati mfumukazi.’
Koma sunaganizire zinthu izi
kapena kusinkhasinkha za mmene ziti zidzathere.
“Ndipo tsopano, tamvera, iwe wongokonda zokondweretsawe,
amene ukukhala mosatekesekawe,
umaganiza mu mtima mwako kuti,
‘Ine ndi Ine, ndipo kupatula ine palibenso wina.
Sindidzakhala konse mkazi wamasiye,
ndipo ana anga sadzamwalira.’
Koma mʼkamphindi, ndiponso tsiku limodzi,
zinthu ziwiri izi zidzakuchitikira:
ana ako kukufera komanso kukhala mkazi wamasiye.
Zimenezi zidzakuchitikira kwathunthu
ngakhale ali ndi amatsenga ambiri
ndi mawula amphamvu.
Iwe unkadalira kuyipa kwako
ndipo unati, ‘Palibe amene akundiona.’
Kuchenjera ndi nzeru zako zidzakusokoneza,
choncho ukuganiza mu mtima mwako kuti,
‘Ine ndine basi, ndipo kupatula ine palibenso wina.’
Ngozi yayikulu idzakugwera
ndipo sudzadziwa momwe ungayipewere ndi matsenga ako.
Mavuto adzakugwera
ndipo sudzatha kuwachotsa;
chipasupasu chimene iwe sukuchidziwa
chidzakugwera mwadzidzidzi.
“Pitiriza tsono kukhala ndi matsenga ako,
pamodzi ndi nyanga zako zochulukazo,
wakhala ukuzigwiritsa ntchito kuyambira ubwana wako.
Mwina udzatha kupambana
kapena kuopsezera nazo adani ako.
Malangizo onse amene unalandira angokutopetsa basi!
Abwere patsogolopa anthu amene amatanthauzira za kumwamba kuti adzakupulumutseni.
Abwere amene amayangʼana nyenyezi, ndi kumalosera mwezi ndi mwezi
zimene ziti zidzakuchitikire.
Ndithudi, anthuwo ali ngati phesi;
adzapsa ndi moto.
Sangathe kudzipulumutsa okha
ku mphamvu ya malawi a moto.
Awa si makala a moto woti wina nʼkuwotha;
kapena moto woti wina nʼkuwukhalira pafupi.
Umu ndi mmene adzachitire amatsenga,
anthu amene wakhala ukugwira nawo ntchito
ndi kuchita nawo malonda chiyambire cha ubwana wako.
Onse adzamwazika ndi mantha,
sipadzakhala ndi mmodzi yemwe wokupulumutsa.”
Israeli ndi Nkhutukumve
“Mverani izi, inu nyumba ya Yakobo,
inu amene amakutchani dzina lanu Israeli,
ndinu a fuko la Yuda,
inu mumalumbira mʼdzina la Yehova,
ndi kupemphera kwa Mulungu wa Israeli,
ngakhale osati mʼchoonadi kapena mʼchilungamo.
Komabe inu mumadzitcha nzika za mzinda wopatulika
ndipo mumadalira Mulungu wa Israeli,
amene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse:
Zimene zinachitika poyamba ndinalosera kalekale,
zinatuluka mʼkamwa mwanga ndipo ndinazilengeza;
tsono mwadzidzidzi ndinachitapo kanthu ndipo zinachitikadi.
Pakuti Ine ndinadziwa kuti iwe ndiwe nkhutukumve
wa nkhongo gwaa,
wa mutu wowuma.
Ine ndinakuwuziratu zinthu izi kalekale lomwe;
zisanachitike ndinazilengezeratu kwa iwe
kuti unganene kuti,
‘Fano langa ndilo lachita zimenezi,
kapena kuti fano langa losema ndi kamulungu kanga kachitsulo ndiwo analamula kuti zimenezi zichitike.’
Inu munamva zinthu zimenezi.
Kodi inu simungazivomereze?
“Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ndidzakuwuzani zinthu zatsopano
zinthu zobisika zimene simunazidziwe konse.
Zinthu zimenezi zikulengedwa tsopano lino, osati kalekale;
munali musanazimve mpaka lero lino.
Choncho inu simunganene kuti,
‘Zimenezi ndiye ayi, ndinazidziwa kale.’
Inu simunazimvepo kapena kuzidziwa;
makutu anu sanali otsekuka.
Tsono Ine ndinadziwa bwino kuti ndinu anthu achiwembu ndi kuti
chiyambire ubwana wanu munatchedwa owukira.
Ine ndikuchedwetsa mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.
Ndikukulezerani ukali wanga kuti anthu andilemekeze.
Sindidzakuwonongani kotheratu.
Taonani, ndinakuyeretsani ngati siliva;
ndinakuyesani mʼngʼanjo yamasautso.
Chifukwa cha ulemu wanga, chifukwa cha ulemu wanga Ine ndikuchita zimenezi.
Ndingalole bwanji kuti ndinyozeke?
Ulemerero wanga sindidzawupereka kwa wina.
Kumasulidwa kwa Israeli
“Tamvera Ine, iwe Yakobo,
Israeli, amene ndinakuyitana:
Mulungu uja Woyamba
ndi Wotsiriza ndine.
Inde dzanja langa linamanga maziko a dziko lapansi,
dzanja langa lamanja linafunyulula mlengalenga.
Ndi mawu anga ndinalenga kumwamba
ndi dziko lapansi.
“Sonkhanani pamodzi inu nonse ndipo mvetserani:
Ndani mwa mafano anu amene analoseratu za zinthu izi?
Wokondedwa wa Yehova uja adzachita
zomwe Iye anakonzera Babuloni;
dzanja lake lidzalimbana ndi Kaldeya.
Ine, Inetu, ndayankhula;
ndi kumuyitana
ndidzamubweretsa ndine
ndipo adzakwaniritsa zolinga zake.
“Bwerani pafupi ndipo mvetserani izi:
“Kuyambira pachiyambi sindinayankhule mobisa;
pa nthawi imene zinkachitika zimenezi Ine ndinali pomwepo.”
Ndipo tsopano Ambuye Yehova wandipatsa Mzimu wake
ndi kundituma.
Yehova, Mpulumutsi wanu,
Woyerayo wa Israeli akuti,
“Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndimakuphunzitsa kuti upindule,
ndimakutsogolera pa njira yoyenera kuyitsata.
Ngati iwe ukanangosamalira zolamulira zanga,
bwenzi mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje,
ndi chipulumutso chako ngati mafunde a pa nyanja.
Zidzukulu zako zikanachuluka ngati mchenga,
ana ako akanachuluka ngati fumbi;
dzina lawo silikanachotsedwa pamaso panga
ndipo silikanafafanizidwa konse.”
Tulukani mʼdziko la Babuloni!
Thawani dziko la Kaldeya!
Lengezani zimenezi ndi mawu a chisangalalo
ndipo muzilalikire
mpaka kumathero a dziko lapansi;
muzinena kuti, “Yehova wawombola Yakobo mtumiki wake.”
Iwo sanamve ludzu pamene Yehova ankawatsogolera mʼchipululu;
anawapatsa madzi otuluka mʼthanthwe;
anangʼamba thanthwelo ndipo
munatuluka madzi.
“Palibe mtendere kwa anthu ochimwa,” akutero Yehova.
Mtumiki wa Yehova
Mverani Ine, inu anthu a pa zilumba
tcherani khutu, inu anthu a mayiko akutali:
Yehova anandiyitana ine ndisanabadwe,
ananditchula dzina ndili mʼmimba ya amayi anga.
Iye anasandutsa pakamwa panga kukhala ngati lupanga lakuthwa,
anandibisa mu mthunzi wa dzanja lake;
Iye anandisandutsa ngati muvi wakuthwa
ndipo anandibisa mʼchimake.
Iye anati kwa ine, “Ndiwe mtumiki wanga, Israeli.
Anthu adzanditamanda chifukwa cha iwe.”
Koma Ine ndinati, “Ine ndinkaganiza kuti ndinagwira ntchito
ndi kuwononga mphamvu zanga pachabe,
koma ayi, zondiyenera zili mʼmanja a Yehova,
ndipo mphotho yanga ili mʼmanja mwa Mulungu wanga.”
Yehova anandiwumba ine
mʼmimba mwa amayi anga kuti ndikhale mtumiki wake
kuti ndibweze fuko la Yakobo kwa Iye
ndi kusonkhanitsa Israeli kwa Iye,
choncho ndimalemekezeka mʼmaso mwa Yehova,
ndipo ndimapeza mphamvu mwa Mulungu wanga.
Yehovayo tsono akuti,
“Nʼchinthu chochepa kwambiri kwa iwe kuti ukhale mtumiki wanga,
kuti udzutse mafuko a Yakobo
ndi kuwabweretsa kwawo Aisraeli amene anapulumuka.
Choncho iwe udzakhala ngati chowunikira,
udzafikitsa uthenga wa chipulumutso changa ku mathero a dziko lapansi.”
Yehova Mpulumutsi ndi Woyerayo wa Israeli akuyankhula,
Woyerayo wa Israeli akunena,
amene mitundu ya anthu inamuda,
amenenso anali kapolo wa mafumu ankhanza uja kuti,
“Mafumu adzaona ntchito ya chipulumutso changa ndipo adzayimirira.
Akalonga nawonso adzagwada pansi.
Zimenezi zidzachitika chifukwa cha Yehova amene ndi wokhulupirika
ndi Woyerayo wa Israeli amene wakusankha iwe.”
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
Yehova akuti,
“Pa nthawi imene ndinakukomera mtima ndinakuyankha,
ndipo pa tsiku lachipulumutso ndinakuthandiza;
ndinakusunga ndi kukusandutsa
kuti ukhale pangano kwa anthu,
kuti dziko libwerere mwakale
ndi kuti cholowa changa chowonongeka chija ndichigawegawenso.
Ndidzawuza a mʼndende kuti atuluke
ndi a mu mdima kuti aonekere poyera.
“Adzapeza chakudya mʼmphepete mwa njira
ndi msipu pa mʼmalo owuma.
Iwo sadzamva njala kapena ludzu,
kutentha kwa mʼchipululu kapena dzuwa silidzawapsereza;
chifukwa Iye amene amawachitira chifundo adzawatsogolera
ndi kuwaperekeza ku akasupe a madzi.
Mapiri anga onse ndidzawasandutsa njira yoyendamo,
ndipo misewu yanga yayikulu ndidzayikweza.
Taonani, anthu anga adzachokera kutali,
ena kumpoto, ena kumadzulo,
enanso adzachokera ku chigawo cha Asuwani.”
Imbani mwachimwemwe, inu zolengedwa zamlengalenga;
kondwera, iwe dziko lapansi;
imbani nyimbo inu mapiri!
Pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,
ndipo wachitira chifundo anthu ake ovutika.
Koma Ziyoni anati, “Yehova wandisiya,
Ambuye wandiyiwala.”
“Kodi amayi angathe kuyiwala mwana wawo wakubere
ndi kusachitira chifundo mwana amene anabereka iwo eni?
Ngakhale iye angathe kuyiwala,
Ine sindidzakuyiwala iwe!
Taona, ndakulemba iwe mʼzikhantho zanga;
makoma ako ndimawaona nthawi zonse.
Amisiri odzakumanganso akubwerera mofulumira,
ndipo amene anakupasula akuchokapo.
Kweza maso ako ndipo uyangʼaneyangʼane
ana ako onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe.
Yehova akuti, ‘Ine Yehova wamoyo,
anthu ako adzakhala ngati chinthu chodzikongoletsa
chimene mkwatibwi wavala pa mkono pake.’
“Ngakhale unasanduka bwinja ndi kuwonongedwa
ndipo dziko lako ndi kusakazidwa,
chifukwa cha kuchuluka kwa anthu malo okhalamo adzakhala operewera
ndipo amene anakuwononga iwe aja adzakhala kutali.
Ana obadwa nthawi yako yachisoni
adzanena kuti,
‘Malo ano atichepera,
tipatse malo ena woti tikhalemo.’
Tsono iwe udzadzifunsa kuti,
‘Kodi ndani anandiberekera ana amenewa?
Ana anga onse anamwalira ndipo sindinathenso kukhala ndi ana ena;
ndinapita ku ukapolo ndipo ndinachotsedwa.
Ndani anawalera ana amenewa?
Ndinatsala ndekha,
nanga awa, achokera kuti?’ ”
Zimene Ambuye Yehova akunena ndi izi,
“Taonani, Ine ndidzakodola Anthu a mitundu ina kuti abwere.
Ndidzawakwezera anthu a mitundu ina mbendera yanga kuti abwere.
Tsono adzabwera ndi ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja mwawo
ndipo adzanyamula ana ako aakazi pa mapewa awo.
Mafumu adzakhala abambo wongokulera
ndipo akazi a mafumu adzakhala amayi wongokulera.
Iwo adzagwetsa nkhope
zawo pansi.
Ndiye inu mudzazindikira kuti Ine ndine Yehova;
iwo amene amadalira Ine sadzakhumudwa.”
Kodi mungathe kulanda anthu ankhondo zofunkha zawo,
kapena kupulumutsa anthu ogwidwa mʼdzanja la munthu wankhanza?
Koma zimene Yehova akunena ndi izi,
“Ankhondo adzawalanda amʼndende awo,
ndipo munthu woopsa adzamulanda zofunkha zawo;
ndidzalimbana ndi amene amalimbana nanu,
ndipo ndidzapulumutsa ana anu.
Anthu amene anakuponderezani adzadya mnofu wawo omwe;
adzamwa magazi awo omwe ngati aledzera ndi vinyo.
Zikadzatero anthu onse adzadziwa
kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wanu,
Momboli wanu, Wamphamvu wa Yakobo.”
Tchimo la Israeli, Kumvera kwa Mtumiki
Yehova akuti,
“Kalata imene ndinasudzulira amayi
anu ili kuti?
Kapena mwa anthu amene ndili nawo ngongole,
ndinakugulitsani kwa ati?
Inu munagulitsidwa ku ukapolo chifukwa cha machimo anu;
amayi anu anachotsedwa chifukwa cha kulakwa kwanu.
Nʼchifukwa chiyani pamene ndinabwera kudzakupulumutsani panalibe munthu?
Pamene ndinayitana, nʼchifukwa chiyani panalibe wondiyankha?
Kodi dzanja langa ndi lalifupi kuti nʼkulephera kukuwombolani?
Kodi ndilibe mphamvu zokupulumutsirani?
Ndi kudzudzula kokha ndinawumitsa nyanja yayikulu,
mitsinje ndinayisandutsa chipululu;
nsomba za mʼmenemo zinawola chifukwa chosowa madzi;
ndipo zinafa ndi ludzu.
Ndinaphimba thambo ndi mdima
ndipo chiguduli chinakhala chofunda chake.”
Ambuye Yehova anandiphunzitsa mawu oyenera kuyankhula
kudziwa mawu olimbitsa mtima anthu ofowoka.
Mmawa mulimonse amandidzutsa,
amathwetsa khutu langa kuti ndimve monga amachitira munthu amene akuphunzira.
Ambuye Yehova wanditsekula makutu anga,
ndipo sindinakhale munthu wowukira
ndipo sindinabwerere mʼmbuyo.
Ndinapereka msana wanga kwa ondimenya
masaya anga ndinawapereka kwa anthu ondizula ndevu;
sindinawabisire nkhope yanga
anthu ondinyoza ndi ondilavulira.
Popeza Ambuye Yehova amandithandiza,
sindidzachita manyazi.
Tsono ndalimba mtima ngati msangalabwi,
chifukwa ndikudziwa kuti sindidzachita manyazi.
Wondikhalira kumbuyo ali pafupi,
ndaninso amene adzandiyimba mlandu?
Abwere kuti tionane maso ndi maso!
Mdani wanga ndi ndani?
Abweretu kuti tilimbane!
Ambuye Yehova ndiye amene amandithandiza.
Ndaninso amene adzanditsutsa?
Onse adzatha ngati chovala
chodyedwa ndi njenjete.
Ndani mwa inu amaopa Yehova
ndi kumvera mawu a mtumiki wake?
Aliyense woyenda mu mdima,
popanda chomuwunikira,
iye akhulupirire dzina la Yehova
ndi kudalira Mulungu wake.
Koma tsopano inu nonse amene mumasonkha moto
ndi kuyatsa sakali za moto kufuna kuwononga anzanu,
lowani mʼmoto wanu womwewo.
Pitani mu sakali za moto zimene mwayatsa.
Ndipo ine Yehova
ndiye amene ndidzakugwetsereni mazunzowo.
Chipulumutso Chamuyaya cha Ziyoni
“Mverani Ine, inu amene mukufuna chipulumutso
ndiponso amene mumafunafuna Yehova:
Taganizani za thanthwe kumene munasemedwa
ndipo ku ngwenya kumene anakukumbani;
taganizani za Abrahamu, kholo lanu,
ndi Sara, amene anakubalani.
Pamene ndinkamuyitana nʼkuti alibe mwana,
koma ndinamudalitsa ndi kumupatsa ana ambiri.
Yehova adzatonthozadi Ziyoni,
ndipo adzachitira chifundo mabwinja ake onse;
Dziko lake la chipululu adzalisandutsa ngati Edeni,
malo ake owuma ngati munda wa Yehova.
Anthu adzayimba nyimbo zonditamanda
ndi kundiyamika.
“Mverani Ine, anthu anga:
tcherani khutu, inu mtundu wanga:
malangizo adzachokera kwa Ine;
cholungama changa chidzawunikira anthu a mitundu yonse.
Ndili pafupi kubwera kudzawombola anthu anga.
Ndidzabwera mofulumira ngati kuwunika kudzapulumutsa anthu anga;
ndipo ndidzalamulira anthu a mitundu yonse.
Mayiko akutali akundiyembekezera.
Iwo akudikira kuti ndidzawapulumutse.
Kwezani maso anu mlengalenga,
yangʼanani pansi pa dziko;
mlengalenga udzazimirira ngati utsi,
dziko lapansi lidzatha ngati chovala
ndipo anthu ake adzafa ngati nsabwe.
Koma chipulumutso changa chidzakhala mpaka muyaya,
chilungamo changa chidzakhala cha nthawi zonse.
“Mverani Ine, inu amene mukudziwa choonadi,
anthu inu amene mukusunga malangizo anga mʼmitima yanu;
musaope kudzudzulidwa ndi anthu
kapena kuopsezedwa akamakulalatirani.
Pakuti njenjete idzawadya ngati chovala;
mbozi idzawadya ngati thonje.
Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka muyaya,
chipulumutso changa chidzakhala mpaka mibadomibado.”
Dzambatukani, dzambatukani! Valani zilimbe,
Inu Yehova;
dzambatukani, monga munkachitira masiku amakedzana,
monga nthawi ya mibado yakale.
Si ndinu kodi amene munaduladula Rahabe,
amene munabaya chinjoka cha mʼnyanja chija?
Kodi sindinu amene munawumitsa nyanja yayikulu,
madzi ozama kwambiri aja?
Kodi sindinu amene munapanga njira pa madzi ozama,
kuti anthu amene munawapulumutsa awoloke powuma?
Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera
nakafika ku Ziyoni nyimbo ili pakamwa;
chimwemwe chamuyaya chizidzaonekera pa nkhope zawo.
Adzakhala ndi chikondwerero ndi chimwemwe,
chisoni ndi kubuwula zidzathawa.
Yehova akuti, “Ndinetu amene ndimakutonthozani mtima.
Chifukwa chiyani mukuopa munthu woti adzafa?
Mukuopa munthu woti monga udzu sadzakhalitsa.
Koma inu mumayiwala Yehova Mlengi wanu,
amene anayala za mlengalenga
ndi kuyika maziko a dziko lapansi.
Inu nthawi zonse mumaopsezedwa
chifukwa cha ukali wa anthu okuponderezani
amene angofuna kukuwonongani.
Kodi uli kuti tsopano ukali wa anthu okuponderezaniwo?
Amʼndende adzamasulidwa posachedwa;
sadzalowa mʼmanda awo,
kapena kusowa chakudya.
Pakuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndimavundula nyanja kotero mafunde ake amakokoma.
Dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Ndayika mawu anga mʼkamwa mwanu
ndipo ndakuphimbani ndi mthunzi wa dzanja langa.
Ine ndimayika pa malo pake zinthu za mlengalenga,
ndipo ndinayika maziko a dziko lapansi,
ndimawuza anthu a ku Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’ ”
Kutha kwa Mavuto A Yerusalemu
Dzambatuka, dzambatuka!
Imirira iwe Yerusalemu.
Iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo
chimene Yehova anakupatsa.
Iwe amene unagugudiza
chikho chochititsa chizwezwe.
Mwa ana onse amene anabereka,
panalibe ndi mmodzi yemwe anamutsogolera;
mwa ana onse amene analera,
panalibe ndi mmodzi yemwe anamugwira dzanja.
Mavuto awiriwa akugwera iwe.
Dziko lako lasakazika ndi kuwonongeka. Anthu afa ndi njala ndi lupanga.
Ndani angakumvere chisoni?
Ndani angakutonthoze?
Ana ako akomoka;
ali lambalamba pa msewu,
ngati mphoyo yogwidwa mu ukonde.
Ukali wa Yehova
ndi chidzudzulo chake zidzawagwera.
Nʼchifukwa chake imva izi iwe amene ukuvutika,
iwe amene waledzera, koma osati ndi vinyo.
Ambuye Yehova wanu,
Mulungu amene amateteza anthu ake akuti,
“Taona, ndachotsa mʼdzanja lako
chikho chimene chimakuchititsa kudzandira;
sudzamwanso chikho
cha ukali wanga.
Ndidzapereka chikhocho kwa anthu amene amakuzunza,
amene ankakuwuza kuti,
‘gona pansi tikuyende pa msana.’
Ndipo msana wako anawuyesa pansi popondapo,
ngati msewu woti ayendepo.”
Dzambatuka, dzambatuka iwe Ziyoni,
vala zilimbe.
Vala zovala zako zokongola,
iwe Yerusalemu, mzinda wopatulika.
Pakuti kuyambira tsopano anthu osachita mdulidwe ndi odetsedwa
sadzalowanso pa zipata zako.
Sasa fumbi lako;
imirira nukhale pa mpando waufumu, iwe Yerusalemu.
Inu omangidwa a ku Ziyoni,
masulani maunyolo amene ali mʼkhosi mwanumo.
Pakuti Yehova akuti,
“Sindinalandirepo kanthu pamene ndinakugulitsani,
choncho mudzawomboledwa wopanda ndalama.”
Pakuti Ambuye Yehova akuti,
“Poyamba paja anthu anga anapita kukakhala ku Igupto;
nawonso Asiriya awapondereza popanda chifukwa.”
Tsopano Ine Yehova ndikuti,
“Kodi nditani pakuti anthu anga atengedwa ukapolo osaperekapo kanthu,
amene amawalamulira amawanyoza,”
akutero Yehova.
“Ndipo tsiku lonse, akungokhalira
kuchita chipongwe dzina langa.
Tsono tsiku limenelo anthu anga adzadziwa dzina langa;
kotero adzadziwa
kuti ndi Ine amene ndikuyankhula,
Indedi, ndine.”
Ngokongoladi mapazi a
amithenga obweretsa nkhani yabwino amene akuyenda pa mapiri.
Iwo akukubweretserani nkhani zabwino za mtendere,
chisangalalo ndi chipulumutso.
Iwo akubwera kudzawuza anthu
a ku Ziyoni kuti,
“Mulungu wako ndi mfumu!”
Mverani! Alonda anu akukweza mawu awo;
akuyimba pamodzi mwachimwemwe.
Popeza akuona chamaso
kubwera kwa Yehova ku Yerusalemu.
Imbani pamodzi mofuwula nyimbo zachimwemwe,
inu mabwinja a Yerusalemu,
pakuti Yehova watonthoza mtima anthu ake,
wapulumutsa Yerusalemu.
Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatulika
pamaso pa anthu a mitundu yonse,
ndipo anthu onse a dziko lapansi
adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.
Nyamukani, nyamukani, chokaniko ku Babuloniko!
Musakhudze kanthu kodetsedwa!
Inu amene mumanyamula ziwiya za Yehova
tulukanimo ndipo mudziyeretse.
Koma simudzachoka mofulumira
kapena kuchita chothawa;
pakuti Yehova adzayenda patsogolo panu,
Mulungu wa Israeli adzakutetezani kumbuyo kwanu.
Kuzunzika ndi Ulemerero wa Mtumiki
Taonani, mtumiki wanga adzapambana pa ntchito yake
adzakwezedwa ndi kulemekezedwa ndipo adzalandira ulemu waukulu kwambiri.
Anthu ambiri atamuona anadzidzimuka,
chifukwa nkhope yake inali itasakazika; sinalinso ngati ya munthu.
Ndipo thupi lake linasakazika; silinalinso ngati la munthu.
Momwemonso anthu a mitundu yonse adzadodoma naye,
ndipo mafumu adzatseka pakamwa pawo kusowa chonena chifukwa cha iye.
Pakuti zinthu zimene iwo sanawuzidwepo, adzaziona,
ndipo zimene sanazimvepo, adzazimvetsa.
Ndani wakhulupirira zimene tanenazi;
kapena ndani amene Yehova wamuzindikiritsa mphamvu zake?
Iye anakula ngati mphukira pamaso pake,
ndiponso ngati muzu mʼnthaka yowuma.
Iye analibe thupi labwino kapena nkhope yokongola yoti ife nʼkumamuchewukira,
analibe maonekedwe woti ife nʼkumamukhumbira.
Iye ananyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu,
munthu amene moyo wake unali wamasautso, wozolowera zowawa,
ndipo anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.
Iye ananyozedwa, ndipo ife sitinamuyese kanthu.
Ndithudi, iye anamva zowawa mʼmalo mwa ife;
ndipo anasautsidwa mʼmalo mwathu.
Koma ife tinkaganiza kuti ndi Mulungu amene akumulanga,
kumukantha ndi kumusautsa.
Koma iye analasidwa chifukwa cha zolakwa zathu,
ndipo anamuzunza chifukwa cha zoyipa zathu;
iye analangidwa kuti ife tikhale ndi mtendere,
ndipo ndi mabala ake ife tinachiritsidwa.
Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera,
aliyense mwa ife akungodziyendera;
ndipo Yehova wamusenzetsa
zoyipa zathu zonse.
Anthu anamuzunza ndi kumusautsa,
koma sanayankhule kanthu.
Monga mwana wankhosa wopita naye kokamupha amachitira,
kapena monga nkhosa imakhalira duu poyimeta,
momwemonso iye sanatsekule pakamwa pake.
Atatha kumugwira mwankhanza ndikumuyimba mlandu, kenaka anapita naye kukamupha.
Ndipo ndani amene analabadirako za zidzukulu zake,
poona kuti iye anachotsedwa mʼdziko la anthu amoyo?
Ndani anaganizirapo poona kuti iye anakanthidwa chifukwa cha zolakwa za anthu anga?
Anamukonzera manda ake pamodzi ndi anthu oyipa
ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi anthu achuma,
ngakhale kuti iye sanachite za chiwawa,
kapena kuyankhula za chinyengo.
Komatu ndi Yehova amene anafuna kuti amuzunze ndi kumusautsa.
Yehova anapereka moyo wa mtumiki wake kuti ukhale nsembe yoperekedwa chifukwa cha zolakwa.
Tsono iye adzaona zidzukulu zake ndipo adzakhala ndi moyo wautali,
ndipo chifuniro cha Yehova chidzachitika mwa iye.
Atatha mazunzo a moyo wake,
adzaona kuwala, ndipo adzakhutira.
Mwa nzeru zake mtumiki wanga wolungamayo adzalungamitsa anthu ambiri,
popeza adzasenza zolakwa zawo.
Motero Ine ndidzamupatsa ulemu pamodzi ndi akuluakulu,
adzagawana zofunkha ndi ankhondo amphamvu,
popeza anapereka moyo wake mpaka kufa,
ndipo anamuyika mʼgulu la anthu olakwa kuti akhululukidwe.
Pakuti iye anasenza machimo a anthu ambiri,
ndipo anawapempherera anthu olakwa.
Ulemerero Wamʼtsogolo wa Ziyoni
“Sangalala, iwe mayi wosabala,
iwe amene sunabalepo mwana;
imba nyimbo, ndi kufuwula mwachimwemwe,
iwe amene sunamvepo ululu wa pobereka;
chifukwa mkazi wosiyidwa adzakhala ndi ana ambiri
kuposa mkazi wokwatiwa,”
akutero Yehova.
Kulitsa malo omangapo tenti yako,
tambasula kwambiri nsalu zake,
usaleke;
talikitsa zingwe zako,
limbitsa zikhomo zako.
Pakuti udzasendeza malire ako kumanja ndi kumanzere;
ndipo zidzukulu zako zidzalanda dziko la anthu a mitundu ina
ndipo zidzakhala mʼmizinda yawo yosiyidwa.
“Usachite mantha; sadzakunyozanso.
Usakhumudwe; sudzapeputsidwanso.
Udzayiwala za manyazi zimene zinakuchitikira nthawi ya unyamata wako
ndipo za manyazi zimene zinakuchitikira pa nthawi ya umasiye wako sudzazikumbukanso.
Pakuti Mlengi wako ali ngati mwamuna wako,
dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
Woyerayo wa Israeli ndiye Mpulumutsi wanu;
dzina lake ndi Mulungu wa dziko lonse lapansi.
Yehova wakuyitananso,
uli ngati mkazi wosiyidwa ndi wodzaza ndi chisoni mu mtima,
mkazi amene anakwatiwa pa unyamata wake kenaka nʼkukanidwa,”
akutero Mulungu wako.
“Kwa kanthawi kochepa, Ine ndinakusiya,
koma ndidzakutenganso chifukwa ndimakukonda kwambiri.
Ndinakufulatira kwa kanthawi kochepa
ndili wokwiya kwambiri.
Koma ndi kukoma mtima kwanga kwa muyaya,
ndidzakuchitira chifundo,”
akutero Yehova Mpulumutsi wako.
“Kwa ine zimenezi zili ngati mmene zinalili mʼnthawi ya Nowa.
Monga ndinalumbira nthawi imeneyo kuti sindidzawononganso dziko lapansi ndi madzi.
Kotero tsopano ndalumbira kuti sindidzakupseraninso mtima,
sindidzakudzudzulaninso.
Ngakhale mapiri atagwedezeka
ndi zitunda kusunthidwa,
koma chikondi changa chosasinthika pa iwe sichidzatha.
Pangano langa lamtendere silidzasintha,”
akutero Yehova amene amakuchitira chifundo.
“Iwe mzinda wozunzika, wokunthidwa ndi namondwe ndiponso wopanda wokutonthoza,
Ine ndidzakongoletsa miyala yako.
Maziko ako ndidzamanga ndi miyala ya safiro.
Ndidzamanga nsanja zako zankhondo ndi miyala yokongola ya rubi.
Ndidzamanga zipata zako ndi miyala yonyezimira ngati moto,
ndipo linga lako lonse lidzakhala la miyala yamtengowapatali.
Yehova adzaphunzitsa ana ako onse,
ndipo ana ako adzakhala ndi mtendere wochuluka.
Udzakhazikika mʼchilungamo chenicheni:
Sudzakhalanso wopanikizika,
chifukwa sudzaopa kanthu kalikonse.
Sudzakhalanso ndi mantha
chifukwa manthawo sadzafika pafupi ndi iwe.
Ngati wina adzakuthirani nkhondo, si ndine amene ndachititsa;
aliyense amene adzalimbana nanu adzagonja chifukwa cha iwe.
“Taona, ndi Ine amene ndinalenga munthu wosula zitsulo
amene amakoleza moto wamakala
ndi kusula zida zoti azigwiritse ntchito.
Ndipo ndine amene ndinalenga munthu wosakaza kuti awononge;
palibe chida chopangidwa ndi mdani chimene chidzakupweteke,
ndipo onse okuneneza pa mlandu udzawatsutsa.
Umu ndimo adzapezekere atumiki a Yehova.
Chipambano chawo chichokera kwa Ine,”
akutero Yehova.
Kuyitanidwa kwa Womva Ludzu
“Bwerani, inu nonse amene muli ndi ludzu,
bwerani madzi alipo;
ndipo inu amene mulibe ndalama
bwerani, mudzagule chakudya kuti mudye!
Bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka
osalipira ndalama, osalipira chilichonse.
Chifukwa chiyani ndalama zanu mukuwonongera zinthu zimene samadya,
ndipo mukuwononga malipiro anu pa zinthu zimene sizikhutitsa?
Tamverani, mvetsetsani zimene ndikunena kuti mudye zimene zili zabwino;
ndipo mudzisangalatse.
Tcherani makutu ndipo mubwere kwa Ine;
mvereni Ine, kuti mukhale ndi moyo.
Ndidzachita nanu pangano losatha,
chikondi changa chija chosasinthika ndi chodalirika ndinalonjeza Davide.
Taonani, ine ndamusankha kuti akhale mboni yanga kwa mitundu ya anthu,
kuti akhale mtsogoleri ndi wolamulira mitundu ya anthu.
Ndithu inu mudzayitanitsa mitundu ya anthu imene simuyidziwa,
ndipo mitundu ya anthu imene sikudziwani idzabwera ndi liwiro kwa inu.
Izi zidzatero chifukwa Yehova Mulungu wanu,
Woyerayo wa Israeli,
wakuvekani ulemerero.”
Funafunani Yehova pamene Iye akupezeka.
Mupemphere kwa Iye pamene ali pafupi.
Woyipa asiye makhalidwe ake oyipa,
ndipo wosalungama asinthe maganizo ake oyipa.
Abwerere kwa Yehova, ndipo adzamuchitira chifundo,
ndi kwa Mulungu wathu, pakuti adzamukhululukira koposa.
“Pakuti maganizo anga siwofanana ndi maganizo anu,
ngakhale njira zanu si njira zanga,”
akutero Yehova.
“Monga momwe mlengalenga muli kutali ndi dziko lapansi,
momwemonso zochita zanga nʼzolekana kutali ndi zochita zanu,
ndipo maganizo anga ndi osiyana kutali ndi maganizo anu.
Monga mvula ndi chisanu chowundana
zimatsika kuchokera kumwamba,
ndipo sizibwerera komweko
koma zimathirira dziko lapansi.
Ndipo zimameretsa ndi kukulitsa zomera
kenaka nʼkupatsa mlimi mbewu ndi chakudya.
Ndi mmenenso amachitira mawu ochokera mʼkamwa mwanga.
Sadzabwerera kwa Ine kopanda phindu lake,
koma adzachita zonse zimene ndifuna,
ndipo adzakwaniritsa cholinga chimene ndinawatumira.
Inu mudzatuluka mu mzindawo mwachimwemwe
ndipo adzakutsogolerani mwamtendere;
mapiri ndi zitunda
zidzakuyimbirani nyimbo,
ndipo mitengo yonse yamʼthengo
idzakuwombereni mʼmanja.
Mʼmalo mʼmene tsopano muli mitengo ya minga mudzamera mitengo ya payini,
ndipo kumene kuli mkandankhuku kudzamera mchisu.
Zimenezi zidzakhala chikumbutso cha Yehova,
ngati chizindikiro chamuyaya,
chimene sichidzafafanizika konse.”
Chipulumutso kwa Anthu Ena Onse
Yehova akuti,
“Chitani chilungamo
ndi zinthu zabwino,
chifukwa chipulumutso changa chili pafupi
ndipo ndidzakuwombolani posachedwapa.
Ndi wodala munthu amene amachita zimenezi,
munthu amene amalimbika kuzichita,
amene amasunga Sabata osaliyipitsa,
ndipo amadziletsa kuchita zoyipa.”
Mlendo amene waphatikana ndi Yehova asanene kuti,
“Ndithu Yehova wandichotsa pakati pa anthu ake.”
Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti,
“Ine ndine mtengo wowuma basi.”
Popeza Yehova akuti,
“Wofulidwa amene amasunga masabata anga,
nachita zokomera Ine
ndi kusunga pangano langa,
ndidzawapatsa dzina ndi mbiri yabwino
mʼkati mwa Nyumba yanga ndi makoma ake,
kuposa kukhala ndi ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzawapatsa dzina labwino,
losatha ndi losayiwalika.”
Yehova akuti, “Alendo amene amadziphatika kwa Yehova,
motero kuti amamutumikira Iye,
amakonda dzina la Yehova,
amamugwirira ntchito,
komanso kusunga Sabata osaliyipitsa
ndi kusunga bwino pangano langa,
amenewa Ine ndidzawafikitsa ku phiri langa lopatulika,
ndidzawapatsa chimwemwe mʼnyumba yanga ya mapemphero.
Zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo
ndidzazilandira pa guwa langa la nsembe.
Paja nyumba yanga idzatchedwa
nyumba ya mapemphero ya anthu a mitundu yonse.”
Ambuye Yehova, amene amasonkhanitsa
Aisraeli onse ali ku ukapolo akunena kuti,
“Ndidzasonkhanitsano anthu ena
kuwonjezera amene anasonkhana kale.”
Mulungu Adzazula Anthu Oyipa
Bwerani, inu zirombo zonse zakuthengo,
inu nonse zirombo zamʼnkhalango bwerani mudzadye!
Atsogoleri onse a Israeli ndi akhungu,
onse ndi opanda nzeru;
onse ndi agalu opanda mawu,
samatha kuwuwa:
amagona pansi nʼkumalota
amakonda kugona tulo.
Ali ngati agalu amene ali ndi njala yayikulu;
sakhuta konse.
Abusa nawonso samvetsa zinthu;
onse amachita monga akufunira,
aliyense amafunafuna zomupindulitsa iye mwini.
Aliyense amafuwulira mnzake kuti, “Bwera, tiye timwe vinyo!
Tiyeni timwe mowa mpaka kukhuta!
Mawa lidzakhala ngati leroli,
kapena kuposa lero lino.”
Anthu olungama amafa,
ndipo palibe amene amalingalira mu mtima mwake;
anthu odzipereka amatengedwa,
ndipo palibe amene amamvetsa chifukwa chake.
Anthu olungama amatengedwa
kuti tsoka lisawagwere.
Iwo amene amakhala moyo wolungama
amafa mwamtendere;
amapeza mpumulo pamene agona mu imfa.
“Bwerani kuno, anthu ochita zoyipa,
inu muli ngati zidzukulu za mkazi wachigololo ndi wadama!
Kodi inu mukuseka yani?
Kodi mukumunena ndani
ndi kupotoza pakamwa panu?
Kodi inu si ana owukira,
zidzukulu za anthu abodza?
Inu mumapembedza mafano pamene mumalobodoka ndi zilakolako zanu pakati pa mitengo ya thundu,
ndiponso pa tsinde pa mtengo uliwonse wa nthambi zambiri.
Mumapereka ana anu ngati nsembe mu zigwa
ndiponso mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe.
Mafano a pakati pa miyala yosalala ya mu zigwa ndiye chuma chanu. Inde, ndiye gawo lanu.
Mumapereka chopereka cha chakumwa kwa mafanowo,
ndipo mumaperekanso chopereka cha chakudya.
Kodi zimenezi
zingandichititse kuti ndikukomereni mtima?
Inu munayiwala bedi lanu pa phiri lalitali ndi looneka kutali.
Mumapita kumeneko kukapereka nsembe zanu.
Mʼnyumba mwanu mwayika
mafano kuseri kwa zitseko ndiponso pa mphuthu.
Mwandisiya Ine, mwavula zovala zanu.
Bedi lanu mwalikulitsa ndipo mwakwera ndi zibwenzi zanu,
ndiye mwazilipira kuti mugone nazo.
Kumene mwakwaniritsa zilakolako zanu zoyipa.
Mumapita kukapembedza fano la Moleki mutatenga mafuta
ndi zonunkhira zochuluka.
Munachita kutumiza akazembe anu kutali;
inu ngakhale munapita ku manda kwenikweniko!
Inu mumatopa ndi maulendo anu,
koma simunathe kunena kuti, ‘Nʼzopanda phindu.’
Munapezako kumeneko zokhumba zanu
nʼchifukwa chake simunalefuke.
“Kodi ndani amene mwachita naye mantha ndi kumuopa,
kotero kuti mwakhala mukundinamiza,
ndipo Ine simundikumbukira nʼkomwe,
kapena kuganizirapo mʼmitima yanu za Ine?
Kodi mwaleka kundiopa chifukwa choti
ndakhala chete nthawi yayitali?
Koma ndaonetsa poyera ntchito zanu zomwe mumati nʼzolungama,
ndi mafano anu kuti nʼzosathandiza.
Pamene mufuwula kupempha thandizo,
mafano anu amene munasonkhanitsawo ndiyetu akupulumutseni!
Mphepo idzanyamula mafano anu onsewo,
mpweya chabe udzawulutsa mafanowo.
Koma munthu amene amadalira ine
adzalandira dziko lokhalamo.
Phiri langa lopatulika lidzakhala lakelake.”
Mpumulo kwa Anthu Osweka Mtima
Ndipo panamveka mawu akuti,
“Undani, undani, konzani msewu!
Chotsani zotchinga pa njira yoyendamo anthu anga.”
Pakuti Iye amene ali Wamkulu ndi Wopambanazonse,
amene alipo nthawi zonse, amene dzina lake ndi Woyerayo,
akunena kuti, “Ndimakhala pamalo aulemu ndi opatulika,
koma ndimakhalanso ndi munthu wodzichepetsa ndi wosweka mtima
kuti odzichepetsawo ndiwalimbitse
ndi kuwachotsa mantha osweka mtima.
Sindidzawatsutsa anthu mpaka muyaya
kapena kuwapsera mtima nthawi zonse,
popeza kuti ndinalenga anthu anga
ndi kuwapatsa mpweya wamoyo.
Ine ndinakwiya kwambiri chifukwa cha tchimo lawo ladyera;
ndinawalanga ndi kuwafulatira mokwiya,
koma iwo anapitirirabe kuchita ntchito zawo zoyipa.
Ndaona zochita zawo, komabe ndidzawachiritsa;
kuwapumulitsa ndi kuwapatsa mtendere,
anthu olira a mu Israeli adzanditamanda ndi milomo yawo.
Anthu amene ali kutali ndi apafupi pomwe ndidzawapatsa mtendere,”
“Ndipo ndidzawachiritsa.”
Akutero Yehova.
Koma anthu oyipa ali ngati nyanja yowinduka,
yosatha kukhala bata,
mafunde ake amaponya matope ndi ndere.
“Palibe mtendere kwa oyipa,” akutero Mulungu wanga.
Kusala Kwenikweni
“Fuwula kwambiri, usaleke.
Mawu ako amveke ngati lipenga.
Uwawuze anthu anga za kulakwa kwawo;
uwuze nyumba ya Yakobo za machimo awo.
Pakuti tsiku ndi tsiku amafunafuna Ine;
amaoneka ngati a chidwi chofuna kudziwa zimene ndimafuna,
kukhala ngati kuti ndi dziko limene limachita zolondola
ndipo silinasiye zolamulira za Mulungu wake.
Amandipempha kuti ndigamule mlandu wawo mwachilungamo
ndipo amaonetsa chidwi chofuna kukhala pafupi ndi Mulungu.
Anthu akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani ife tasala
kudya pamene Inu simukulabadirapo?
Kodi ife tavutikiranji nʼkudzichepetsa
pamene Inu simunasamalepo?’ ”
Yehova akuti, “Komatu tsiku lanu losala kudya, mumachita zinthu zokukondweretsani,
ndipo mumazunza antchito anu onse.
Mumati uku mukusala kudya, uku mukukangana ndi kumenyana,
mpaka kumenyana ndi nkhonya zopweteka.
Kusala kudya mukuchitiramu musayembekezere kuti mawu anu amveka kumwamba.
Kodi kusala kudya kumene ndimakufuna Ine nʼkumeneku,
kungokhala tsiku loti munthu adzichepetse basi?
Kodi ndi tsiku loti munthu angowerama pansi ngati bango
ndi kumayala ziguduli nʼkuthirapo phulusa nʼkugonapo?
Kodi ndiye mumati kusala kudya kumeneko,
tsiku lokondweretsa Yehova?
“Kodi si uku kusala kudya kumene Ine ndimakufuna:
Kumasula maunyolo ozunzizira anthu
ndi kumasula zingwe za goli,
kupereka ufulu kwa oponderezedwa
ndi kuphwanya goli lililonse?
Anthu anjala kodi mwawagawira chakudya chanu?
Osowa ndi ongoyendayenda,
kodi mwawapatsa malo ogona?
Munthu wausiwa kodi mwamupatsa chovala?
Mukatero chipulumutso chanu chidzabwera ngati mʼbandakucha,
ndipo mabala anu adzachira msangamsanga;
chilungamo chanu chidzakutsogolerani
ndipo ulemerero wa Yehova udzakhala chokutchinjirizani kumbuyo kwanu.
Mukamadzapemphera Yehova adzakuyankhani;
mukadzapempha thandizo, Iye adzati: Ine ndili pano.
“Ngati muleka kuzunza anzanu,
ngati musiya kuloza chala ndiponso kunena zoyipa za anzanu.
Ndipo ngati mudyetsa anthu anjala,
ndi kuthandiza anthu oponderezedwa,
pamenepo kuwala kwanu kudzaonekera mu mdima,
ndipo usiku wanu udzakhala ngati usana.
Yehova adzakutsogolerani nthawi zonse;
adzakwaniritsa zosowa zanu mʼdziko longʼalukangʼaluka dzuwa
ndipo adzalimbitsa matupi anu.
Mudzakhala ngati dimba la madzi ambiri,
ngati kasupe amene madzi ake saphwa.
Anthu ako adzamanganso nyumba zimene zakhala mabwinja nthawi yayitali,
ndipo adzamanganso pa maziko akalekale;
inu mudzatchedwa okonza makoma opasuka.
Anthu okonza misewu ndi nyumba zake.
“Muzisunga osaphwanya Sabata;
musamachite zimene mukufuna pa masiku anga opatulika,
tsiku la Sabata lizikhala tsiku lachisangalalo.
Tsiku lopatulika la Yehova muzililemekeza
posayenda mʼnjira zanu,
kapena kuchita zimene mukufuna ndi kuyankhula zopandapake,
mukatero mudzapeza chimwemwe mwa Yehova,
ndipo ndidzakukwezani ndi kukupambanitsani pa dziko lonse lapansi.
Mudzadyerera dziko limene ndinapatsa Yakobo kholo lanu.”
Yehova wayankhula ndi pakamwa pake.
Tchimo, Kuvomereza ndi Chipulumutso
Taonani, mkono wa Yehova si waufupi kuti sungathe kupulumutsa,
kapena khutu lake kuti ndilogontha kuti sangamve.
Koma zoyipa zanu zakulekanitsani
ndi Mulungu wanu;
ndipo wakufulatirani chifukwa cha machimo anu,
kotero Iye sadzamva.
Pakuti manja anu ali psuu ndi magazi.
Munayipitsa zala zanu ndi zamphulupulu.
Pakamwa panu payankhula zabodza,
ndipo lilime lanu lanena zinthu zoyipa.
Palibe amene akuyimba mnzake mlandu molungama,
palibe amene akupita ku mlandu moona mtima.
Iwo amadalira mawu opanda pake ndipo amayankhula mabodza;
amalingalira za mphulupulu ndipo amachita zoyipa.
Iwo amayikira mazira a mamba
ndipo amaluka ukonde wakangawude.
Aliyense amene adzadya mazira awo adzafa,
ndipo ngati dzira limodzi lasweka limatulutsa mphiri.
Ukonde wawo wa kangawude sangawuvale ngati chovala;
ndipo chimene apangacho sangachifunde.
Ntchito zawo ndi zoyipa,
ndipo amakonda kuchita zandewu ndi manja awo.
Amathamangira kukachita zoyipa;
sachedwa kupha anthu osalakwa.
Maganizo awo ndi maganizo oyipa;
kulikonse kumene amapita amasiyako bwinja ndi chiwonongeko.
Iwo sadziwa kuchita za mtendere;
zonse zimene amachita nʼzopanda chilungamo.
Njira zawo zonse nʼzokhotakhota;
aliyense oyenda mʼnjira zimenezo sadzapeza mtendere.
Anthu akuti, “Chifukwa cha zimenezi chilungamo chatitalikira;
ndipo chipulumutso sichitifikira.
Timafunafuna kuwala koma timangopeza mdima okhaokha;
tinayembekezera kuyera koma timayenda mu mdima wandiweyani.
Timapapasapapasa khoma ngati munthu wosaona,
kuyangʼanayangʼana njira ngati anthu opanda maso.
Timapunthwa dzuwa lili paliwombo ngati kuti ndi usiku;
timakhala pansi mu mdima ngati anthu akufa.
Tonse timabangula ngati zimbalangondo:
Timalira modandaula ngati nkhunda.
Tinayembekezera kuweruza kolungama; koma sitikupeza.
Timayembekezera chipulumutso koma chimakhala nafe kutali.”
Pakuti zolakwa zathu nʼzochuluka pamaso panu,
ndipo machimo athu akutsutsana nafe.
Zolakwa zathu zili ndi ife nthawi zonse
ndipo tikuvomereza machimo athu:
Tawukira ndi kumukana Yehova.
Tafulatira Mulungu wathu,
pa kupondereza anzathu ndi kupandukira Yehova,
ndi pa kuyankhula mabodza amene tawaganiza mʼmitima mwathu.
Motero kuweruza kolungama kwalekeka
ndipo choonadi chili kutali ndi ife;
kukhulupirika sikukupezekanso mʼmabwalo a milandu,
ndipo kuona mtima sikukupezekanso mʼmenemo.
Choonadi sichikupezeka kumeneko,
ndipo wina akakana kuchita nawo zoyipa amapeza mavuto.
Yehova anaziona zimenezi ndipo zinamunyansa
kuti panalibe chiweruzo cholungama.
Yehova anaona kuti panalibe ndi mmodzi yemwe,
Iye anadabwa kuti panalibe ndi mmodzi yemwe woti nʼkupembedzera;
Choncho mphamvu zake zomwe zinamuthandiza,
ndipo anadzilimbitsa ndi kulungama kwake;
Iye anavala chilungamo ngati chovala chachitsulo chapachifuwa,
ndipo kumutu kwake amavala chipewa chachipulumutso;
anavala kulipsira ngati chovala
ndipo anadzikuta ndi mkwiyo ngati chofunda.
Iye adzawabwezera chilango adani a anthu ake
molingana ndi zimene anachita,
adzaonetsa ukali kwa adani ake
ndi kubwezera chilango odana naye.
Adzalanga ngakhale okhala mayiko akutali.
Choncho akadzabwera ngati madzi
oyendetsedwa ndi mphepo yamphamvu yamkuntho.
Anthu onse kuyambira kumadzulo mpaka kummawa
adzaopa dzina la Yehova ndi ulemerero wake.
“Mpulumutsi adzabwera ku Ziyoni
kudzapulumutsa anthu a fuko la Yakobo amene analapa machimo awo,”
akutero Yehova.
Yehova akuti, “Kunena za pangano lake ndi iwo, Mzimu wanga umene uli pa inu, ndiponso mawu anga amene ndayika mʼkamwa mwanu sadzachoka mʼkamwa mwanu, kapena kuchoka mʼkamwa mwa ana anu, kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zawo kuyambira tsopano mpaka kalekale,”
akutero Yehova.
Ulemerero wa Ziyoni
“Dzuka, wala, pakuti kuwala kwako kwafika,
ndipo ulemerero wa Yehova wakuwalira.
Taona, mdima waphimba dziko lapansi
ndipo mdima wandiweyani wagwa pa anthu a mitundu ina,
koma Yehova adzakuwalira iwe,
ndipo ulemerero wake udzaoneka pa iwe.
Mitundu ya anthu idzatsata kuwunika kwako
ndipo mafumu adzalondola kunyezimira kwa mʼbandakucha wako.
“Tukula maso ako, yangʼanayangʼana ndipo ona zimene zikuchitika.
Onse akusonkhana ndipo akubwera kwa iwe;
ana ako a amuna akubwera kuchokera kutali
ndipo ana ako aakazi anyamulidwa mʼmanja.
Ukadzaona zimenezi udzasangalala kwambiri,
mtima wako udzalumpha ndi kudzaza ndi chimwemwe;
chuma chakunyanja chidzabwera kwa iwe
chuma cha mitundu ya anthu chidzabwera kwa iwe.
Gulu la ngamira lidzaphimba dziko lako,
ngamira zingʼonozingʼono zidzachokera ku Midiyani ndi ku Efai.
Ndipo onse a ku Seba adzabwera
atanyamula golide ndi lubani
uku akutamanda Yehova.
Ziweto zonse za ku Kedara adzazisonkhanitsa kwa inu,
nkhosa zazimuna za ku Nabayoti zidzakutumikirani;
zidzalandiridwa monga chopereka pa guwa langa la nsembe,
ndipo ndidzakongoletsa Nyumba yanga.
“Kodi ndi zayani izo zikuwuluka ngati mitambo,
ngati kapena nkhunda zobwerera ku zisa zawo?
Ndithu, izi ndi sitima za pa madzi zochokera ku mayiko akutali;
patsogolo pali sitima zapamadzi za ku Tarisisi,
zikubweretsa ana ako ochokera kutali,
pamodzi ndi siliva wawo ndi golide wawo,
kudzalemekeza Yehova Mulungu wako,
Woyerayo wa Israeli,
pakuti Iye wakuvekani inu ulemerero.
“Alendo adzamanganso malinga ako,
ndipo mafumu awo adzakutumikira.
Ngakhale ndinakukantha ndili wokwiya,
koma tsopano ndidzakukomera mtima ndikukuchitira chifundo.
Zipata zako zidzakhala zotsekula nthawi zonse,
sadzazitseka nthawi zonse, usana ndi usiku,
kotero anthu adzabwera kwa iwe ndi chuma chawo,
akuyenda pa mdipiti mafumu awo ali patsogolo.
Pakuti mtundu wa anthu ndi mafumu amene sakutumikira iwe;
adzawonongeka kotheratu.
“Adzabwera nayo kwa iwe mitengo ya payini,
mkuyu ndi naphini imene ili mʼnkhalango ya Lebanoni
kuti adzakongoletsere malo a nyumba yanga yopatulika;
ndipo ndidzalemekeza malo amene Ine ndimapondapo.
Ana aja amene anakuzunzani adzabwera ndipo adzakugwadirani;
onse amene anakunyozani adzagwada pansi pa mapazi anu.
Ndipo adzakutchani kuti Mzinda wa Yehova;
Ziyoni mzinda wa Woyerayo wa Israeli.
“Ngakhale anthu anakusiya nadana nawe,
koma Ine ndidzakukuza mpaka muyaya,
ndipo udzakhala malo a chimwemwe
cha anthu amibado yonse.
Udzamwa mkaka wa mitundu ya anthu
ndi kuleredwa pa maere aufumu,
motero udzadziwa kuti Ine Yehova, ndine Mpulumutsi wako,
Momboli wako ndiye Wamphamvu wa Yakobo.
Ndidzakupatsa golide mʼmalo mwa mkuwa,
ndi siliva mʼmalo mwa chitsulo.
Ndidzakupatsa mkuwa mʼmalo mwa thabwa
ndi chitsulo mʼmalo mwa miyala.
Olamulira ako adzakhala a mtendere.
Ndidzasandutsa okulamulira kuti akhale achilungamo.
Ziwawa sizidzamvekanso mʼdziko lako,
bwinja kapena chiwonongeko sizidzapezeka mʼdziko lako,
ndidzakhala malinga ako okuteteza
ndipo udzanditamanda.
Sipadzakhala dzuwa kuti likuwunikire,
kapena mwezi kuti uwunikire usiku,
pakuti Yehova ndiye adzakhale kuwunika kwako kwa muyaya,
ndipo Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.
Dzuwa lako silidzalowanso,
ndipo mwezi wako sudzazimiriranso;
Yehova adzakhala kuwunika kwako kwamuyaya,
ndipo masiku a mavuto ako adzatha.
Ndipo anthu ako onse adzakhala olungama
ndipo dzikolo lidzakhala lawo mpaka muyaya.
Iwo ndi mphukira imene Ine ndayidzala,
ntchito ya manja anga,
kuti aonetse ulemerero wanga.
Kabanja kakangʼono kadzasanduka fuko,
kafuko kakangʼono kudzasanduka mtundu wamphamvu.
Ine ndine Yehova,
nthawi yake ikafika ndidzazichita zimenezi mofulumira.”
Uthenga Wabwino wa Yehova
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine,
chifukwa Yehova wandidzoza
kuti ndilalikire uthenga wabwino kwa anthu osauka.
Wandituma kuti ndikatonthoze anthu osweka mtima,
ndikalengeze kwa akapolo kuti alandire ufulu
ndiponso kuti ndikamasule a mʼndende.
Wandituma kuti ndikalengeze nthawi imene Yehova adzapulumutsa anthu ake;
za tsiku limene Yehova adzalanga adani a anthu ake.
Wandituma kuti ndikatonthoze olira.
Wandituma kuti ndiwakonzere olira a ku Ziyoni,
nkhata ya maluwa yokongola
mʼmalo mwa phulusa,
ndiwapatse mafuta achikondwerero
mʼmalo mwa kulira.
Ndiwapatse chovala cha matamando
mʼmalo mwa mtima wopsinjika.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ya thundu yamphamvu yachilungamo,
yoyidzala Yehova
kuti Iye mwini apezemo ulemerero wake.
Adzamanganso mabwinja akale a mzinda
ndipo malo amene anawonongeka kalekale aja adzakonzanso.
Adzakonzanso mizinda imene inapasuka,
imene yakhala yowonongeka kwa nthawi yayitali kwambiri.
Anthu achilendo adzakutumikirani; adzazidyetsa ziweto zanu;
iwo adzagwira ntchito mʼminda yanu ya mpesa.
Ndipo inu mudzatchedwa ansembe a Yehova,
adzakutchulani kuti ndinu atumiki a Mulungu wathu.
Mudzadyerera chuma cha mitundu ya anthu,
ndipo mudzanyadira ulemu umene mwalandira.
Chifukwa manyazi awo anali owirikiza;
ndi kuti munalandira
chitonzo ndi kutukwana,
adzakondwera ndi cholowa chawo,
tsono adzalandira cholowa chawo cha chigawo cha dziko mowirikiza,
ndipo chimwemwe chamuyaya chidzakhala chawo.
“Pakuti Ine Yehova, ndimakonda chilungamo;
ndimadana ndi zakuba ndi zoyipa.
Anthu anga ndidzawapatsa mphotho mokhulupirika
ndikupangana nawo pangano losatha.
Ana awo adzakhala odziwika pakati pa mitundu ya anthu
ndipo adzukulu awo adzakhala otchuka pakati pa anthu a mitundu ina.
Aliyense wowaona adzazindikira
kuti ndi anthu amene Yehova wawadalitsa.”
Ine ndikusangalala kwambiri chifukwa cha Yehova;
moyo wanga ukukondwera chifukwa cha Mulungu wanga.
Pakuti Iye wandiveka zovala zachipulumutso,
ndipo wandiveka mkanjo wachilungamo.
Zili ngati mkwati wovala nkhata ya maluwa mʼkhosi mwake,
ndiponso ngati mkwatibwi wovala mikanda yamtengowapatali.
Monga momwe nthaka imameretsa mbewu
ndiponso monga munda umakulitsa mbewu zimene anadzala,
momwemonso Ambuye Yehova adzaonetsa chilungamo ndi matamando
pamaso pa mitundu yonse ya anthu.
Dzina Latsopano la Ziyoni
Chifukwa chokonda Ziyoni sindidzakhala chete,
chifukwa chokonda Yerusalemu sindidzakhala chete,
mpaka chilungamo chake chitaoneka poyera ngati kuwala,
ndi chipulumutso chake chitaoneka ngati sakali yoyaka.
Mitundu ya anthu idzaona iwe utapambana pa nkhondo
ndipo mafumu onse adzaona ulemerero wako.
Adzakuyitanira dzina latsopano
limene adzakupatse ndi Yehova.
Udzakhala ngati chipewa chaulemerero mʼdzanja la Yehova,
ndi ngati nduwira yaufumu mʼdzanja la Mulungu wako.
Sadzakutchanso “Wosiyidwa,”
ndipo dziko lako silidzatchedwanso “Chipululu.”
Koma dzina lako latsopano lidzakhala “Ndakondwera naye.”
Ndipo dziko lako lidzatchedwa “Wokwatiwa.”
Chifukwa Yehova akukondwera nawe,
ndipo adzakhala ngati mwamuna wa dziko lako.
Monga mnyamata amakwatira namwali,
momwenso mmisiri wodzakumanga adzakukwatira;
monga mkwati amakondwera ndi mkwatibwi,
chonchonso Mulungu adzakondwera nawe.
Iwe Yerusalemu, pa malinga ako ndayikapo alonda;
sadzakhala chete usana kapena usiku.
Inu amene mumakumbutsa Yehova za malonjezo ake
musapumule.
Musamupatse mpata wopuma mpaka atakhazikitsa Yerusalemu
kukhala mzinda umene dziko lapansi lidzawutamande.
Yehova analumbira atakweza dzanja lake.
Anati,
“Sindidzaperekanso tirigu wako
kuti akhale chakudya cha adani ako,
ndipo alendo sadzamwanso vinyo wako watsopano
pakuti unamuvutikira.
Koma amene amakakolola ndiwo amene adzadye buledi
ndi kutamanda Yehova,
ndipo amene amasonkhanitsa pamodzi mphesa ndiwo amene adzamwe vinyo
mʼmabwalo a Nyumba yanga.”
Tulukani, dutsani pa zipata!
Konzerani anthu njira.
Lambulani, lambulani msewu waukulu!
Chotsani miyala.
Kwezani mbendera kuti mitundu ya anthu izione.
Yehova walengeza
ku dziko lonse lapansi kuti,
Awuzeni anthu a ku Yerusalemu kuti,
“Taonani, chipulumutso chanu chikubwera;
Yehova akubwera ndi mphotho yake
akubwera nazo zokuyenerani.”
Iwo adzatchedwa Anthu Opatulika,
owomboledwa a Yehova;
ndipo adzakutchani “Okondwa a Yehova”
“Mzinda umene Yehova sanawusiye.”
Yehova Agonjetsa Anthu a Mitundu Ina
Kodi ndani uyo akubwera kuchokera ku Edomu,
atavala zovala za ku Bozira za madontho ofiira?
Kodi uyu ndani, amene wavala zovala zokongola,
akuyenda mwa mphamvu zake?
“Ndi Ineyo, woyankhula zachilungamo
ndiponso wamphamvu zopulumutsa.”
Nanga bwanji zovala zanu zili psuu,
ngati za munthu wofinya mphesa?
“Ndapondereza ndekha anthu a mitundu ina ngati mphesa,
palibe ndi mmodzi yemwe anali nane.
Ndinawapondereza ndili wokwiya
ndipo ndinawapondereza ndili ndi ukali;
magazi awo anadothera pa zovala zanga,
ndipo zovala zanga zonse zinathimbirira.
Pakuti ndinatsimikiza mu mtima mwanga kuti lafika tsiku lolipsira anthu anga;
ndipo chaka cha kuwomboledwa kwanga chafika.
Ndinayangʼana ndipo panalibe munthu wondithandiza.
Ndinadabwa kwambiri kuti panalibe wondichirikiza;
choncho ndinapambana ndi mphamvu zanga,
ndipo mkwiyo wanga unandilimbitsa.
Ndinapondereza mitundu ya anthu ndili wokwiya;
ndipo ndinawasakaza
ndipo ndinathira magazi awo pansi.”
Matamando ndi Pemphero
Ndidzafotokoza za kukoma mtima kwa Yehova,
ntchito zimene Iye ayenera kutamandidwa.
Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha zonse zimene watichitira.
Inde, mwa chifundo ndi kukoma mtima kwake
Yehova wachitira nyumba ya Israeli
zinthu zabwino zambiri.
Yehova anati, “Ndithu awa ndi anthu anga,
ana anga amene sadzandinyenga Ine.”
Choncho anawapulumutsa.
Iyenso anasautsidwa mʼmasautso awo onse,
ndipo mngelo wochokera kwa Iye anawapulumutsa.
Mwa chikondi ndi chifundo chake iye anawapulumutsa,
anawanyamula ndikuwatenga
kuyambira kale lomwe.
Komabe iwo anawukira
ndi kumvetsa chisoni Mzimu Woyera.
Motero Yehova anatembenuka nakhala mdani wawo
ndipo Iye mwini anamenyana nawo.
Pamenepo anthu ake anakumbukira masiku amakedzana,
masiku a Mose mtumiki wake;
ndipo anafunsa kuti, “Ali kuti Yehova amene anawawolotsa pa nyanja,
pamodzi ndi Mose mʼbusa wawo?
Ali kuti Iye amene anayika
Mzimu Woyera pakati pawo?
Ali kuti amene anachita zinthu zodabwitsa
ndi mphamvu zake zazikulu kudzera mwa Mose?
Ali kuti amene anagawa madzi pa nyanja anthu ake akuona,
kuti dzina lake limveke mpaka muyaya,
amene anawayendetsa pa nyanja yozama?
Monga kavalo woyendayenda mʼchipululu,
iwo sanapunthwe;
Mzimu Woyera unawapumulitsa
ngati mmene ngʼombe zimapumulira.
Umu ndi mmene Inu munatsogolera anthu anu
kuti dzina lanu lilemekezeke.”
Inu Yehova amene muli kumwambako, pa mpando wanu wolemekezeka,
wopatulika ndi waulemerero, tiyangʼaneni ife.
Kodi changu chanu ndi mphamvu zanu zili kuti?
Simukutionetsanso kukoma mtima kwanu ndi chifundo chanu.
Koma Inu ndinu Atate athu,
ngakhale Abrahamu satidziwa
kapena Israeli kutivomereza ife;
Inu Yehova, ndinu Atate athu,
kuyambira kale dzina lanu ndinu Mpulumutsi wathu.
Chifukwa chiyani, Inu Yehova, mukutisocheretsa pa njira zanu?
Bwanji mukutilola kuti tikhale owuma mitima kotero kuti sitikukuopaninso?
Bwererani chifukwa cha atumiki anu;
mafuko a anthu amene ali cholowa chanu.
Anthu anu atangokhala pa malo anu opatulika pa kanthawi kochepa,
adani athu anasakaza malo anu opatulika.
Ife tili ngati anthu amene
simunawalamulirepo
ngati iwo amene sanakhalepo anthu anu.
Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
Monga momwe moto umatenthera tchire
ndiponso kuwiritsa madzi,
tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,
ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
kapena kuona
Mulungu wina wonga Inu,
amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
amene amakumbukira njira zanu.
Koma Inu munakwiya,
ife tinapitiriza kuchimwa.
Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;
tonse tafota ngati tsamba,
ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
Palibe amene amapemphera kwa Inu
kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;
pakuti mwatifulatira
ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.
Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,
pakuti tonsefe ndi anthu anu.
Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
yatenthedwa ndi moto
ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?
Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?
Chiweruzo ndi Chipulumutso
“Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;
ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.
Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,
ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
Tsiku lonse ndatambasulira manja anga
anthu owukira aja,
amene amachita zoyipa,
natsatira zokhumba zawo.
Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa
mopanda manyazi.
Iwo amapereka nsembe mʼminda
ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
Amakatandala ku manda
ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.
Amadya nyama ya nkhumba,
ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,
chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’
Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,
ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
“Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;
sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu
chifukwa cha machimo awo
ndi a makolo awo,”
akutero Yehova.
“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri
ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,
Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata
zimene anachita kale.”
Yehova akuti,
“Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa
ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,
popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’
Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;
sindidzawononga onse.
Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,
ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.
Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,
ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,
ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe
kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
“Koma inu amene mumasiya Yehova
ndi kuyiwala phiri langa lopatulika,
amene munamukonzera Gadi chakudya
ndi kuthirira Meni chakumwa,
ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe,
ndipo nonse mudzaphedwa;
chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani,
ndinayankhula koma simunamvere.
Munachita zoyipa pamaso panga
ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”
Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti,
“Atumiki anga adzadya,
koma inu mudzakhala ndi njala;
atumiki anga adzamwa,
koma inu mudzakhala ndi ludzu;
atumiki anga adzakondwa,
koma inu mudzakhala ndi manyazi.
Atumiki anga adzayimba
mosangalala,
koma inu mudzalira kwambiri
chifukwa chovutika mu mtima
ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.
Anthu anga osankhidwa
adzatchula dzina lanu potemberera.
Ambuye Yehova adzakuphani,
koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.
Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo
adzachita zimenezo kwa Mulungu woona;
ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo
adzalumbira mwa Mulungu woona.
Pakuti mavuto akale adzayiwalika
ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
Chilengedwe Chatsopano
“Taonani, ndikulenga
mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.
Zinthu zakale sizidzakumbukika,
zidzayiwalika kotheratu.
Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya
chifukwa cha zimene ndikulenga,
pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa
ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu
ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.
Kumeneko sikudzamvekanso kulira
ndi mfuwu wodandaula.
“Ana sadzafa ali akhanda
ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.
Wamngʼono mwa iwo
adzafa ali ndi zaka 100.
Amene adzalephere kufika zaka 100
adzatengedwa kukhala
wotembereredwa.
Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,
adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,
kapena kudzala ndi ena nʼkudya.
Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo
wautali ngati mitengo.
Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito
ya manja awo nthawi yayitali.
Sadzagwira ntchito pachabe
kapena kubereka ana kuti aone tsoka;
chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,
iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.
Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.
Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,
koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.
Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala
chinthu chopweteka kapena chowononga,”
akutero Yehova.
Chiweruzo ndi Chiyembekezo
Yehova akuti,
“Kumwamba ndi mpando wanga waufumu
ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.
Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire,
ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,
motero zonsezi ndi zanga?”
Akutero Yehova.
“Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:
amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,
ndipo amamvera mawu anga.
Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna
amaphanso munthu,
ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa,
amaphanso galu.
Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya
amaperekanso magazi a nkhumba.
Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso
amapembedzanso fano.
Popeza iwo asankha njira zawozawo,
ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.
Inenso ndawasankhira chilango chowawa
ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija.
Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha,
pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu.
Anachita zoyipa pamaso panga
ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”
Imvani mawu a Yehova,
inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake:
“Abale anu amene amakudani,
ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti,
‘Yehova alemekezeke
kuti ife tione chimwemwe chanu!’
Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
Imvani mfuwu mu mzinda,
imvani phokoso mʼNyumba ya Mulungu!
Limenelo ndi liwu la Yehova,
kulanga adani ake onse.
“Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa
wachira kale;
asanayambe kumva ululu,
wabala kale mwana wamwamuna.
Ndani anamvapo zinthu zoterezi?
Ndani anazionapo zinthu zoterezi?
Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi,
kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi?
Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa
nthawi yomweyo anabereka ana ake.
Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,
koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova.
“Kodi ndingatseke mimba
pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
“Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye,
inu nonse amene mumakonda Yerusalemu,
kondwera nayeni kwambiri,
nonse amene mumamulira.
Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake
ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri
wa mʼmawere
a chitonthozo chake.”
Yehova akuti,
“Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje wa madzi,
ndiponso chuma cha anthu a mitundu ina ngati mtsinje wosefukira.
Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene amayi ake amunyamulira pambalipa,
kapena kumufungata pa miyendo yake.
Monga momwe amayi amasangalatsira mwana wawo,
moteronso Ine ndidzakusangalatsani;
ndipo mudzasangalala chifukwa cha Yerusalemu.”
Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu.
Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu.
Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira
ndi kuti ndimakwiyira adani anga.
Taonani, Yehova akubwera ngati moto,
ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu;
Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake
ndi malawi amoto.
Pakuti Yehova adzalanga anthu onse
ndi moto ndi lupanga,
Yehova adzapha anthu ambiri.
Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”
“Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.
“Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo. Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.
“Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova. “Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova. “Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”