- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
HOSEYA
Hoseya
Hoseya
Hos
Hoseya
Awa ndi mawu amene Yehova anayankhula kwa Hoseya mwana wa Beeri pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda ndiponso pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Yowasi mfumu ya ku Israeli.
Mkazi wa Hoseya ndi Ana Ake
Yehova atayamba kuyankhula kudzera mwa Hoseya, Yehova anati kwa Hoseyayo, “Pita kakwatire mkazi wachiwerewere ndipo ubereke naye ana mʼchiwerewere chake pakuti anthu a mʼdziko muno achimwa pochita chigololo choyipitsitsa, posiya Yehova.” Motero Hoseya anakwatira Gomeri mwana wamkazi wa Dibulaimu, ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna.
Tsono Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti Yezireeli, pakuti ndili pafupi kulanga banja la Yehu chifukwa cha anthu amene anawapha ku Yezireeli ndipo ndidzathetsa ufumu wa Israeli. Tsiku limenelo ndidzathyola uta wa Israeli mʼchigwa cha Yezireeli.”
Gomeri anakhala woyembekezeranso ndipo anabereka mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, “Umutche dzina loti ‘Sakondedwa’ pakuti sindidzaonetsanso chikondi changa pa nyumba ya Israeli, kuti ndingawakhululukire konse. Komatu ndidzaonetsa chikondi pa nyumba ya Yuda; ndipo ndidzawapulumutsa, osati ndi uta, lupanga kapena nkhondo, kapena akavalo ndi okwerapo ake, koma ine Yehova Mulungu wawo ndidzawapulumutsa.”
Sakondedwa ataleka kuyamwa, Gomeri anabereka mwana wina wamwamuna. Pamenepo Yehova anati, “Umutche dzina loti Sianthuanga,” pakuti inu si ndinu anthu anga ndipo Ine si ndine Mulungu wanu.
“Komabe Aisraeli adzachuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja umene sangathe kuwuyeza kapena kuwuwerenga. Pamalo omwe ananena kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ pomweponso adzawatchula kuti ‘Ana a Mulungu wamoyo.’ Anthu a ku Yuda ndi anthu a ku Israeli adzasonkhananso pamodzi ndipo adzasankha mtsogoleri mmodzi ndi kutuluka mʼdzikomo, pakuti tsiku la Yezireeli lidzakhala lalikulu kwambiri.”
“Nena kwa abale ako kuti, ‘Ndinu anthu anga,’ kwa alongo ako kuti ‘Ndinu okondedwa anga.’ ”
Kulangidwa ndi Kubwezeretsedwa kwa Israeli
“Dzudzulani amayi anu, adzudzuleni iwo,
pakuti si mkazi wanga,
ndipo ine sindine mwamuna wake.
Iyeyo achotse maonekedwe adama pa nkhope yake,
ndi kusakhulupirika pa mawere ake.
Akapanda kutero ndidzamuvula,
ndipo adzakhala wamaliseche monga tsiku limene anabadwa;
ndidzamuwumitsa ngati chipululu,
adzakhala ngati dziko lopanda madzi,
ndi kumupha ndi ludzu.
Sindidzaonetsa chikondi changa pa ana ake,
chifukwa ndi ana a mʼchiwerewere.
Amayi awo akhala akuchita zachiwerewere
ndipo anawabereka anawo akuchita zinthu zochititsa manyazi.
Iwo anati, ‘Ine ndidzatsatira zibwenzi zanga,
zimene zimandipatsa chakudya ndi madzi,
ubweya ndi thonje, mafuta ndi chakumwa.’
Choncho njira yake ndidzayitseka ndi minga;
ndidzamuzinga ndi khoma kotero kuti sadzapezanso njira yotulukira.
Adzathamangira zibwenzi zake koma sadzazipeza;
adzazifunafuna koma sadzazipeza.
Pamenepo iye adzati,
‘Ndibwerera kwa mwamuna wanga woyamba uja,
pakuti ndinali pabwino ndi iyeyo kusiyanitsa ndi pano.’
Iye sanazindikire kuti ndine amene
ndinkamupatsa tirigu, vinyo watsopano ndi mafuta.
Ndine amene ndinkamukhuthulira siliva ndi golide,
zimene ankapangira mafano a Baala.
“Choncho Ine ndidzamulanda tirigu wanga pa nthawi yokolola,
ndi vinyo wanga watsopano pa nthawi yopsinya mphesa.
Ndidzamulanda ubweya ndi thonje langa,
zomwe akanaphimba nazo umaliseche wake.
Motero tsopano ndidzaonetsa maliseche ake
pamaso pa zibwenzi zake;
palibe ndi mmodzi yemwe adzamupulumutse mʼmanja mwanga.
Ndidzathetsa zikondwerero zake zonse:
zikondwerero zake za chaka ndi chaka, za mwezi watsopano,
za pa masiku a Sabata ndi maphwando ake onse a pa masiku okhazikitsidwa.
Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa ndi mitengo yake yamkuyu,
imene iye ankanena kuti inali malipiro ake ochokera kwa zibwenzi zake.
Ndidzayisandutsa chithukuluzi,
ndipo zirombo zakuthengo zidzadya zipatsozo.
Ndidzamulanga chifukwa cha masiku
amene anafukiza lubani kwa Abaala;
anadzikongoletsa povala mphete ndi mikanda yamtengowapatali
ndipo anathamangira zibwenzi zake,
koma Ine anandiyiwala,”
akutero Yehova.
“Koma tsopano ndidzamukopa mkaziyo;
ndidzapita naye ku chipululu
ndipo ndidzamuyankhula mwachikondi.
Kumeneko ndidzamubwezera minda yake ya mpesa,
ndipo ndidzasandutsa Chigwa cha Akori kukhala khomo la chiyembekezo.
Kumeneko iye adzayimba nyimbo monga mʼmasiku a ubwana wake,
monga tsiku limene anatuluka ku Igupto.
“Tsiku limeneli,” Yehova akuti,
“udzandiyitana kuti, ‘Amuna anga;’
sudzandiyitananso kuti, ‘Mbuye wanga.’
Ndidzachotsa mayina a Abaala pakamwa pake;
sadzatchulanso mayina awo popemphera.
Tsiku limenelo ndidzachita pangano
ndi zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
ndiponso zolengedwa zokwawa pansi kuti ziyanjane ndi anthu anga.
Ndidzachotsa mʼdzikomo uta,
lupanga ndi zida zonse zankhondo,
kuti onse apumule mwamtendere.
Ndidzakutomera kuti ukhale mkazi wanga mpaka muyaya;
ndidzakutomera mwachilungamo, mwaungwiro,
mwachikondi ndi mwachifundo.
Ndidzakutomera mokhulupirika
ndipo udzadziwa Yehova.
“Tsiku limenelo Ine ndidzayankha,”
akutero Yehova.
“Ndidzayankha mlengalenga pempho lake lofuna mitambo
ndipo mvula idzagwa pa dziko lapansi;
ndipo nthaka idzamvera kupempha kwa tirigu,
vinyo ndi mafuta,
ndipo zidzamvera Yezireeli.
Ndidzadzala Israeli mʼdziko kuti akhale wanga:
ndidzaonetsa chikondi changa kwa anthu amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Sakondedwa.’
Ndidzawawuza amene ndinkawatchula dzina loti, ‘Si anthu anga,’ kuti, ‘Ndinu anthu wanga;’
ndipo adzanena kuti, ‘ndinu Mulungu wathu,’ ”
Hoseya Ayanjana ndi Mkazi Wake
Yehova anati kwa ine, “Pita kamukondenso mkazi wako, ngakhale ali pa chibwenzi ndi wina ndi kuti ndi wachigololo. Mukonde iyeyo monga momwe Yehova amakondera Aisraeli, ngakhale iwo amapita kukapembedza milungu ina ndi kukonda nsembe za keke zamphesa zowuma.”
Motero ndinamukwatira popereka ndalama khumi ndi zisanu zasiliva, ndiponso mitanga isanu ndi iwiri ya barele. Kenaka ndinamuwuza mkaziyo kuti, “Ukhale nane masiku ambiri; usachitenso zachiwerewere kapena chigololo ndi munthu wina, ndipo ine ndidzakhala nawe.”
Pakuti Aisraeli adzakhala masiku ambiri opanda mfumu kapena kalonga, osapereka nsembe kapena kuyimika miyala yachipembedzo, wopanda efodi kapena fano. Pambuyo pake Aisraeli adzabwerera ndi kufunafuna Yehova Mulungu wawo ndi Davide mfumu yawo. Adzabwera kwa Yehova akunjenjemera ndipo adzalandira madalitso mʼmasiku awo otsiriza.
Yehova Ayimba Mlandu Israeli
Inu Aisraeli, imvani mawu a Yehova,
chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi inu
amene mumakhala mʼdzikoli:
“Mʼdziko mwanu mulibe kukhulupirika, mulibe chikondi
mulibe kulabadira za Mulungu.
Muli kutemberera kokha, kunama ndi kupha.
Kuba ndi kuchita chigololo;
machimo achita kunyanya
ndipo akungokhalira kuphana.
Chifukwa chake dziko likulira
ndipo onse amene amakhalamo akuvutika;
zirombo zakuthengo ndi mbalame zamumlengalenga
ndiponso nsomba zamʼnyanja zikufa.
“Koma wina asapeze mnzake chifukwa,
wina aliyense asayimbe mlandu mnzake,
pakuti anthu ako ali ngati anthu
amene amayimba mlandu wansembe.
Mumapunthwa usana ndi usiku
ndipo aneneri amapunthwa nanu pamodzi.
Choncho ndidzawononga amayi anu.
Anthu anga akuwonongeka chifukwa chosadziwa.
“Pakuti mwakana kudziwa,
Inenso ndidzakukanani monga ansembe anga;
chifukwa mwayiwala lamulo la Mulungu wanu,
Inenso ndidzayiwala ana anu.
Ansembe ankati akachuluka
iwo ankandichimwiranso kwambiri;
iwo anasinthanitsa ulemerero wawo ndi chinthu china chonyansa.
Amalemererapo pa machimo a anthu anga
ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo azipitiriza kuchimwa.
Ndipo zidzakhala motere: zochitikira anthu ena, zidzachitikiranso ansembe.
Ndidzawalanga onsewo chifukwa cha njira zawo,
ndidzawabwezera chifukwa cha machitidwe awo.
“Iwo azidzadya koma sadzakhuta;
azidzachita zachiwerewere koma sadzachulukana,
chifukwa anasiya Yehova
kuti adzipereke ku zachiwerewere,
ku vinyo wakale ndi watsopano,
zimene zimachotsa nzeru zomvetsa zinthu
za anthu anga.
Anthu anga amapempha nzeru ku fano lamtengo
ndipo ndodo yawo yamtengo imawayankha.
Mzimu wachiwerewere umawasocheretsa;
iwo sakukhulupirika kwa Mulungu wawo.
Amapereka nsembe pamwamba pa mapiri
ndi kufukiza lubani pa zitunda,
pa tsinde pa mtengo wa thundu, mnjale ndi mkundi,
pamene pali mthunzi wabwino.
Nʼchifukwa chake ana anu aakazi akuchita zachiwerewere
ndipo akazi a ana anu akuchita zigololo.
“Ine sindidzalanga ana anu aakazi
pamene iwo adzachita zachiwerewere,
kapena akazi a ana anu
pamene adzachita zigololo.
Paja inu nomwe amunanu mumayenda ndi akazi achiwerewere,
ndipo mumapereka nsembe pamodzi ndi akazi achiwerewere a ku malo opembedzerako.
Anthu amene alibe nzeru adzawonongeka ndithu!
“Ngakhale umachita chigololo, iwe Israeli,
Yuda asapezeke ndi mlandu wotere.
“Usapite ku Giligala.
Usapite ku Beti-Aveni.
Ndipo usalumbire kuti, ‘Pali Yehova wamoyo!’
Aisraeli ndi nkhutukumve,
ngosamva ngati ana angʼombe.
Kodi Yehova angathe kuwaweta bwanji
ngati ana ankhosa pa msipu wabwino?
Efereimu waphathana ndi mafano;
mulekeni!
Ngakhale pamene zakumwa zawo zatha,
amapitiriza kuchita zachiwerewere;
atsogoleri awo amakonda kwambiri njira zawo zochititsa manyazi.
Adzachotsedwa ndi kamvuluvulu
ndipo adzachita manyazi chifukwa cha nsembe zawo.
Chiweruzo cha Israeli
“Ansembe inu, imvani izi!
Inu Aisraeli, tcherani khutu!
Inu nyumba yaufumu, mvetserani!
Chiweruzo ichi ndi chotsutsa inu:
Inu munali ngati msampha ku Mizipa,
munali ngati ukonde woyalidwa pa phiri la Tabori.
Owukira azama mʼmoyo wakupha,
Ine ndidzawalanga onsewo.
Ndimadziwa zonse za Efereimu;
Aisraeli ndi osabisika kwa Ine.
Efereimu wayamba tsopano kuchita zachiwerewere;
Israeli wadziyipitsa.
“Ntchito zawo siziwalola
kubwerera kwa Mulungu wawo.
Mʼmitima mwawo muli mzimu wachiwerewere;
Iwo sadziwa Yehova.
Kudzikuza kwa Israeli kwakhala umboni womutsutsa;
Aisraeli, ngakhale Aefereimu, anagwa mʼmachimo awo;
Yudanso anagwa nawo pamodzi.
Pamene adzapita ndi nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo
kukapereka nsembe kwa Yehova,
iwo sadzamupeza;
Iye wawachokera.
Iwo ndi osakhulupirika kwa Yehova;
amabereka ana amʼchigololo
ndipo chikondwerero chawo cha mwezi watsopano
chidzawawononga pamodzi ndi minda yawo.
“Womba lipenga mu Gibeya,
liza mbetete mu Rama.
Fuwulani mfuwu wankhondo mu Beti-Aveni;
iwe Benjamini tsogolera.
Efereimu adzasanduka bwinja
pa tsiku la chilango.
Ine ndikulengeza zomwe zidzachitikadi
pakati pa mafuko a Israeli.
Atsogoleri a Yuda ali ngati anthu
amene amasuntha miyala ya mʼmalire.
Ndidzawakhutulira ukali wanga
ngati madzi a chigumula.
Efereimu waponderezedwa,
akulangidwa chifukwa chotsatira
mafano.
Ine ndili ngati njenjete kwa Efereimu,
ngati chinthu chowola kwa anthu a ku Yuda.
“Efereimu ataona nthenda yake,
ndi Yuda ataona zilonda zake,
pamenepo Efereimu anatembenukira kwa Asiriya,
ndipo anawatumizira mfumu yayikulu kudzawathandiza.
Koma mfumuyo singathe kukuchizani,
singathe kuchiritsa mabala anu.
Pakuti Ine ndidzakhala ngati mkango kwa Efereimu.
Ngati mkango wamphamvu kwa Yuda.
Ndidzawakhadzula nʼkuchokapo;
ndidzawatenga ndipo palibe amene adzawalanditse.
Ndipo ndidzabwerera ku malo anga
mpaka anthu anga atavomereza kulakwa kwawo.
Ndipo iwo adzafunafuna nkhope yanga;
mʼmasautso awo adzandifunitsitsa Ine.”
Kusalapa kwa Israeli
“Bwerani, tiyeni tibwerere kwa Yehova.
Iye watikhadzula,
koma adzatichiritsa.
Iye wativulaza,
koma adzamanga mabala athu.
Pakapita masiku awiri adzatitsitsimutsa;
pa tsiku lachitatu Iye adzatiukitsa
kuti tikhale ndi moyo pamaso pake.
Tiyeni timudziwe Yehova,
tiyeni tilimbike kumudziwa Iye.
Adzabwera kwa ife mosakayikira konse
ngati kutuluka kwa dzuwa;
adzabwera kwa ife ngati mvula ya mʼchilimwe,
ngati mvula ya nthawi yamphukira imene imakhathamiritsa nthaka.”
Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani?
Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda?
Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa,
ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.
Choncho ndakuwazani ngati nkhuni kudzera mwa aneneri anga,
ndakuphani ndi mawu a pakamwa panga;
chigamulo changa chinangʼanima ngati mphenzi pa inu.
Pakuti Ine ndimafuna chifundo osati nsembe,
ndi kudziwa Mulungu kulekana ndi nsembe zopsereza.
Monga Adamu, anthuwa aphwanya pangano langa,
iwo sanakhulupirike kwa Ine.
Giliyadi ndi mzinda wa anthu ochita zoyipa,
okhala ndi zizindikiro za kuphana.
Monga momwe mbala zimadikirira anthu,
magulu a ansembe amachitanso motero;
iwo amapha anthu pa njira yopita ku Sekemu,
kupalamula milandu yochititsa manyazi.
Ndaona chinthu choopsa kwambiri
mʼnyumba ya Israeli.
Kumeneko Efereimu akuchita zachiwerewere,
ndipo Israeli wadzidetsa.
“Kunenanso za iwe Yuda,
udzakolola chilango.
“Pamene ndiwabwezere anthu anga zinthu zabwino.”
Pamene ndichiritsa Israeli,
machimo a Efereimu amaonekera poyera
ndiponso milandu ya Samariya sibisika.
Iwo amachita zachinyengo,
mbala zimathyola nyumba,
achifwamba amalanda anthu katundu mʼmisewu.
Koma sazindikira kuti Ine
ndimakumbukira zoyipa zawo zonse.
Azunguliridwa ndi zolakwa zawo;
ndipo sizichoka mʼmaso mwanga.
“Anthuwa amasangalatsa mfumu ndi zoyipa zawozo,
akalonga amasekerera mabodza awo.
Onsewa ndi anthu azigololo,
otentha ngati moto wa mu uvuni,
umene wophika buledi sasonkhezera
kuyambira pamene akukanda buledi mpaka atafufuma.
Pa tsiku la chikondwerero cha mfumu yathu
akalonga amaledzera ndi vinyo,
ndipo amalowa mʼgulu la anthu achipongwe.
Mitima yawo ili ngati uvuni;
amayandikira Mulungu mwachiwembu.
Ukali wawo umanyeka usiku wonse,
mmawa umayaka ngati malawi a moto.
Onsewa ndi otentha ngati uvuni,
amapha olamulira awo.
Mafumu awo onse amagwa,
ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amandiyitana Ine.
“Efereimu wasakanikirana ndi mitundu ya anthu ena;
Efereimu ndi buledi amene wapsa mbali imodzi.
Alendo atha mphamvu zake,
koma iye sakuzindikira.
Tsitsi lake layamba imvi
koma iye sakudziwa.
Kunyada kwake Israeli kukumutsutsa,
koma pa zonsezi
iye sakubwerera kwa Yehova Mulungu wake
kapena kumufunafuna.
“Efereimu ali ngati nkhunda
yopusa yopanda nzeru.
Amayitana Igupto
namapita ku Asiriya.
Akamadzapita, ndidzawakola ndi ukonde wanga;
ndidzawagwetsa pansi ngati mbalame zamumlengalenga.
Ndikadzamva kuti asonkhana pamodzi
ndidzawakola.
Tsoka kwa iwo,
chifukwa andisiya Ine!
Chiwonongeko kwa iwo,
chifukwa andiwukira!
Ndimafunitsitsa kuwapulumutsa
koma amayankhula za Ine monama.
Iwo salirira kwa Ine kuchokera pansi pa mtima,
koma amalira mofuwula ali pa bedi pawo.
Amadzichekacheka chifukwa chofuna tirigu ndi vinyo watsopano,
koma amandifulatira.
Ine ndinawaphunzitsa ndikuwalimbitsa,
koma amandikonzera chiwembu.
Iwo satembenukira kwa Wammwambamwamba;
ali ngati uta woonongeka.
Atsogoleri awo adzaphedwa ndi lupanga
chifukwa cha mawu awo achipongwe.
Motero iwo adzasekedwa
mʼdziko la Igupto.
Israeli Akolola Kamvuluvulu
“Ika lipenga pakamwa pako.
Ngati chiwombankhanga, kutsutsana ndi nyumba ya Yehova
chifukwa anthu aphwanya pangano langa
ndiponso agalukira lamulo langa.
Israeli akulirira kwa Ine kuti,
‘Inu Mulungu wathu, ife timakudziwani!’
Koma Israeli wakana zabwino;
mdani adzamuthamangitsa.
Amalonga mafumu mosatsata kufuna kwanga.
Amasankha akalonga popanda chilolezo changa.
Amadzipangira mafano
asiliva ndi agolide
koma adzawonongeka nawo.
Iwe Samariya, taya fano lako la mwana wangʼombe!
Mkwiyo wanga wayakira anthuwo.
Padzapita nthawi yayitali chotani asanasinthike kukhala oyera mtima?
Mafanowa ndi ochokera ku Israeli!
Mwana wa ngʼombe uyu anapangidwa ndi munthu waluso;
si Mulungu amene anamupanga.
Adzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswa,
mwana wangʼombe wa ku Samariya.
“Aisraeli amadzala mphepo
ndipo amakolola kamvuluvulu.
Tirigu alibe ngala;
sadzabala chakudya.
Akanabala chakudya
alendo akanadya chakudyacho.
Israeli wamezedwa,
tsopano ali pakati pa anthu a mitundu ina
ngati chinthu cha chabechabe.
Pakuti iwo anapita ku Asiriya
ngati mbidzi yongodziyendera pa yokha.
Efereimu wadzigulitsa kwa zibwenzi zake.
Ngakhale wadzigulitsa pakati pa mitundu ya anthu,
Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi.
Iwo adzayamba kuzunzika pansi pa
ulamuliro wankhanza wa mfumu yamphamvu.
“Ngakhale Efereimu anamanga maguwa ambiri a nsembe zoperekedwa chifukwa cha tchimo,
maguwa amenewa akhala malo ochimwirapo.
Ndinawalembera zinthu zambiri za malamulo anga,
koma iwo anaziyesa ngati zinthu zachilendo.
Amapereka nsembe za nyama kwa Ine
ndipo iwo amadya nyamayo,
koma Yehova sakondwera nazo.
Tsopano Iye adzakumbukira zoyipa zawo
ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo:
iwowo adzabwerera ku Igupto.
Israeli wayiwala Mlengi wake
ndipo wamanga nyumba zaufumu;
Yuda wachulukitsa mizinda ya malinga.
Koma Ine ndidzaponya moto pa mizinda yawoyo,
moto umene udzatenthe malinga awo.”
Chilango cha Israeli
Iwe Israeli, usakondwere;
monga imachitira mitundu ina.
Pakuti wakhala wosakhulupirika kwa Mulungu wako;
umakonda malipiro a chiwerewere
pa malo aliwonse opunthira tirigu.
Malo opunthira tirigu ndi malo opsinyira mphesa sadzadyetsa anthu;
adzasowa vinyo watsopano.
Sadzakhalanso mʼdziko la Yehova.
Efereimu adzabwerera ku Igupto
ndipo mudzadya chakudya chodetsedwa ku Asiriya.
Iwo sadzaperekanso chopereka cha chakumwa kwa Yehova,
kapena nsembe zawo kuti akondweretse Yehovayo.
Nsembe zotere zidzakhala kwa iwo ngati chakudya cha anamfedwa;
onse akudya chakudya chimenechi adzakhala odetsedwa.
Chakudya ichi chidzakhala chodya okha,
sichidzalowa mʼnyumba ya Yehova.
Kodi mudzachita chiyani pa tsiku la maphwando anu oyikika;
pa masiku a zikondwerero za Yehova?
Ngakhale iwo atathawa chiwonongeko,
Igupto adzawasonkhanitsa,
ndipo Mefisi adzawayika mʼmanda.
Khwisa adzamera pa ziwiya zawo zasiliva,
ndipo minga idzamera mʼmatenti awo.
Masiku achilango akubwera,
masiku obwezera ali pafupi.
Israeli adziwe zimenezi.
Chifukwa machimo anu ndi ochuluka kwambiri
ndipo udani wanu pa Mulungu ndi waukulu kwambiri.
Mneneri amamuyesa chitsiru,
munthu wanzeru za kwa Mulungu ngati wamisala.
Mneneri pamodzi ndi Mulungu wanga
ndiwo alonda a Efereimu,
koma mneneri amutchera misampha mʼnjira zake zonse,
ndipo udani ukumudikira mʼnyumba ya Mulungu wake.
Iwo azama mu zachinyengo
monga masiku a Gibeya.
Mulungu adzakumbukira zolakwa zawo
ndipo adzawalanga chifukwa cha machimo awo.
“Pamene ndinamupeza Israeli
zinali ngati kupeza mphesa mʼchipululu.
Nditaona makolo anu,
zinali ngati ndikuona nkhuyu zoyambirira kupsa.
Koma atafika ku Baala Peori,
anadzipereka ku fano lija lochititsa manyazi
ndipo anakhala onyansa ngati chinthu chimene anachikondacho.
Ulemerero wa Efereimu udzawuluka ngati mbalame.
Sipadzakhalanso kubereka ana, kuyembekezera kapena kutenga pathupi.
Ngakhale atalera ana
ndidzachititsa kuti mwana aliyense amwalire.
Tsoka kwa anthuwo
pamene Ine ndidzawafulatira!
Ndaona Efereimu ngati Turo,
atadzalidwa pa nthaka ya chonde.
Koma Efereimu adzatsogolera
ana ake kuti akaphedwe.”
Inu Yehova, muwapatse.
Kodi mudzawapatsa chiyani?
Apatseni mimba yomangopita padera
ndi mawere owuma.
“Chifukwa cha zoyipa zawo zonse ku Giligala,
Ine ndinawada kumeneko.
Chifukwa cha machitidwe awo auchimo,
ndidzawapirikitsa mʼnyumba yanga.
Sindidzawakondanso;
atsogoleri awo onse ndi owukira.
Efereimu wathedwa,
mizu yake yauma
sakubalanso zipatso.
Ngakhale atabereka ana,
Ine ndidzapha ana awo okondedwawo.”
Mulungu wanga adzawakana
chifukwa sanamumvere Iye;
adzakhala oyendayenda pakati pa anthu a mitundu ina.
Israeli anali mpesa wotambalala;
anabereka zipatso zambiri.
Pamene zipatso zawo zinanka zichuluka,
anawonjezera kumanga maguwa ansembe.
Pamene dziko lake linkatukuka,
anakongoletsa miyala yake yopatulika.
Mtima wawo ndi wonyenga
ndipo tsopano ayenera kulangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo.
Yehova adzagumula maguwa awo ansembe
ndi kuwononga miyala yawo yopatulika.
Pamenepo anthuwo adzanena kuti, “Ife tilibe mfumu
chifukwa sitinaope Yehova.
Koma ngakhale tikanakhala ndi mfumu,
kodi mfumuyo ikanatichitira chiyani?”
Mafumu amalonjeza zambiri,
amalumbira zabodza
pochita mapangano.
Kotero maweruzo amaphuka
ngati zitsamba zakupha mʼmunda umene walimidwa.
Anthu amene amakhala mu Samariya akuchita mantha
chifukwa cha fano la mwana wangʼombe ku Beti-Aveni.
Anthu ake adzalirira fanolo,
chimodzimodzinso ansembe ake adamawo,
amene anakondwera ndi kukongola kwake,
chifukwa lachotsedwa pakati pawo ndi kupita ku ukapolo.
Fanolo lidzatengedwa kupita ku Asiriya
ngati mphatso kwa mfumu yayikulu.
Efereimu adzachititsidwa manyazi
chifukwa cha mafano ake amitengo.
Samariya ndi mfumu yake adzatengedwa kupita kutali
ngati kanthambi koyenda pa madzi.
Malo opembedzerako mafano a ku Aveni adzawonongedwa.
Ili ndiye tchimo la Israeli.
Minga ndi mitungwi zidzamera
ndi kuphimba maguwa awo ansembe.
Kenaka anthu adzawuza mapiri kuti, “Tiphimbeni!”
ndipo adzawuza zitunda kuti, “Tigwereni!”
“Iwe Israeli, wachimwa kuyambira mʼmasiku a Gibeya,
ndipo wakhala uli pomwepo.
Kodi nkhondo sinagonjetse anthu
ochita zoyipa ku Gibeya?
Pamene ndifunire, ndidzalanga anthuwo;
mitundu ya anthu idzasonkhanitsidwa kudzalimbana nawo,
kuwayika mʼndende chifukwa cha uchimo wawo waukulu.
Efereimu ndi mwana wangʼombe wamkazi wophunzitsidwa
amene amakonda kupuntha tirigu,
choncho Ine ndidzayika goli
mʼkhosi lake lokongolalo.
Ndidzasenzetsa Efereimu goli,
Yuda ayenera kulima,
ndipo Yakobo ayenera kutipula.
Mufese nokha chilungamo
ndipo mudzakolola chipatso cha chikondi changa chosasinthika.
Ndipo tipulani munda wanu wosalimidwawo;
pakuti ino ndi nthawi yofunafuna Yehova,
mpaka Iye atabwera
kudzakugwetserani mivumbi ya chilungamo.
Koma inu munadzala zolakwa,
mwakolola zoyipa;
mwadya chipatso cha chinyengo.
Chifukwa mumadalira mphamvu zanu
ndiponso ankhondo anu ochulukawo,
phokoso lankhondo lidzamveka pakati pa anthu anga
kotero kuti malinga anu onse adzawonongeka,
monga momwe Salimani anawonongera Beti-Aribeli pa nthawi ya nkhondo;
pamene anapha amayi pamodzi ndi ana awo omwe.
Momwemonso zidzakuchitikira, iwe Beteli
chifukwa kuyipa kwako ndi kwakukulu.
Tsiku limeneli likadzafika,
mfumu ya Israeli idzawonongedwa kwathunthu.
Chikondi cha Mulungu pa Israeli
“Israeli ali mwana, ndinamukonda,
ndipo ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.
Koma ndimati ndikamapitiriza kuyitana
iwo amandithawa kupita kutali.
Ankapereka nsembe kwa Abaala
ndipo ankafukiza lubani kwa mafano.
Ndi Ine amene ndinaphunzitsa Efereimu kuyenda,
ndipo ndinawagwira pa mkono;
koma iwo sanazindikire
kuti ndine amene ndinawachiritsa.
Ndinawatsogolera ndi zingwe zachifundo cha anthu
ndi zomangira za chikondi;
ndinachotsa goli mʼkhosi mwawo
ndipo ndinawerama nʼkuwadyetsa.
“Sadzabwerera ku Igupto,
koma Asiriya ndiye adzakhala mfumu yawo
pakuti akana kutembenuka.
Malupanga adzangʼanima mʼmizinda yawo,
ndipo adzawononga mipiringidzo ya zipata zawo
nadzathetseratu malingaliro awo.
Anthu anga atsimikiza zondifulatira Ine.
Ngakhale atayitana Wammwambamwamba,
sizidzatheka kuti Iye awakwezenso.
“Kodi ndingakusiye bwanji iwe Efereimu?
Kodi ndingakupereke bwanji iwe Israeli?
Kodi ndingakuchitire bwanji zimene ndinachitira Adima?
Kodi ndingathe bwanji kukuchitira zimene ndinachitira Zeboimu?
Mtima wanga wakana kutero;
chifundo changa chonse chikusefukira.
Sindidzalola kuti ndikulange ndi mkwiyo wanga woopsa,
kapena kutembenuka ndi kuwononga Efereimu.
Pakuti Ine ndine Mulungu osati munthu,
Woyerayo pakati panu.
Sindidzabwera mwaukali.
Iwo adzatsatira Yehova;
Iye adzabangula ngati mkango.
Akadzabangula,
ana ake adzabwera akunjenjemera kuchokera kumadzulo.
Adzabwera akunjenjemera
ngati mbalame kuchokera ku Igupto,
ngati nkhunda kuchokera ku Asiriya.
Ine ndidzawakhazikanso mʼnyumba zawo,”
akutero Yehova.
Tchimo la Israeli
Efereimu wandizungulira ndi mabodza,
nyumba ya Israeli yandizungulira ndi chinyengo.
Ndipo Yuda wawukira Mulungu,
wawukira ngakhale Woyerayo amene ndi wokhulupirika.
Efereimu amadya mpweya;
tsiku lonse amasaka mphepo ya kummawa
ndipo amachulukitsa mabodza ndi chiwawa.
Amachita mgwirizano ndi Asiriya
ndipo amatumiza mphatso za mafuta a olivi ku Igupto.
Yehova akuyimba mlandu Yuda;
Iye adzalanga Yakobo molingana ndi makhalidwe ake,
adzamulanga molingana ndi ntchito zake.
Akali mʼmimba mwa amayi ake, Yakobo anagwira chidendene cha mʼbale wake;
iye atakula analimbana ndi Mulungu.
Yakobo analimbana ndi mngelo ndipo anapambana;
analira napempha kuti amukomere mtima.
Mulungu anakumana naye ku Beteli
ndipo anayankhula naye kumeneko,
Yehova Mulungu Wamphamvuzonse,
Yehova ndiye dzina lake lotchuka!
Koma inu muyenera kubwerera kwa Mulungu wanu;
pitirizani chikondi ndi chiweruzo cholungama,
ndipo muzidikira Mulungu wanu nthawi zonse.
Munthu wamalonda amagwiritsa ntchito masikelo achinyengo;
iyeyo amakonda kubera anthu.
Efereimu amadzitama ponena kuti,
“Ndine wolemera kwambiri; ndili ndi chuma chambiri.
Palibe amene angandiloze chala
chifukwa cha kulemera kwanga.”
“Ine ndine Yehova Mulungu wako
amene ndinakutulutsa mu Igupto.
Ndidzakukhazikaninso mʼmatenti,
monga munkachitira masiku aja pa nthawi ya zikondwerero zanu.
Ndinayankhula ndi aneneri,
ndinawaonetsa masomphenya ambiri,
ndipo ndinawawuza mafanizo kudzera mwa iwo.”
Kodi Giliyadi ndi woyipa?
Anthu ake ndi achabechabe!
Kodi amapereka nsembe za ngʼombe zazimuna ku Giligala?
Maguwa awo ansembe adzakhala ngati milu ya miyala
mʼmunda molimidwa.
Yakobo anathawira ku dziko la Aramu,
Israeli anagwira ntchito kuti apeze mkazi,
ndipo anaweta nkhosa kuti akwatire mkaziyo.
Yehova anagwiritsa ntchito mneneri kuti atulutse Israeli mu Igupto;
kudzera mwa mneneriyo Iye anawasamalira.
Koma Efereimu wamukwiyitsa kwambiri.
Nʼchifukwa chake Yehova adzawalanga ndi imfa.
Adzawalanga chifukwa anamuchititsa manyazi kwambiri.
Mkwiyo wa Yehova pa Israeli
Kale Efereimu ankati akayankhula, anthu ankanjenjemera;
anali wolemekezeka mu Israeli.
Koma analakwa popembedza Baala, motero anafa.
Tsopano akunka nachimwirachimwirabe;
akudzipangira mafano pogwiritsa ntchito siliva wawo,
zifanizo zopangidwa mwaluso,
zonsezo zopangidwa ndi amisiri.
Amanena za anthu awa kuti,
“Amatenga munthu ndi kumupereka nsembe
ndipo amapsompsona fano la mwana wangʼombe.”
Choncho adzakhala ngati nkhungu yammawa,
ngati mame amene amakamuka msanga,
ngati mungu wowuluka kuchokera pa malo opunthira tirigu,
ngati utsi umene ukutulukira pa zenera.
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
amene ndinakutulutsani mu Igupto.
Simuyenera kudziwa Mulungu wina, koma Ine ndekha,
palibe Mpulumutsi wina kupatula Ine.
Ndinakusamalira mʼchipululu,
mʼdziko lotentha kwambiri.
Pamene ndinawadyetsa, iwo anakhuta;
iwo atakhuta anayamba kunyada;
ndipo anandiyiwala Ine.
Motero ndidzawalumphira ngati mkango,
ndidzawabisalira mu msewu ngati kambuku.
Ngati chimbalangondo cholandidwa ana ake,
ndidzawambwandira ndi kuwathyolathyola.
Ndidzawapwepweta ngati mkango;
chirombo chakuthengo chidzawakhadzula.
“Iwe Israeli, wawonongedwa,
chifukwa ukutsutsana ndi Ine, ukutsutsana ndi mthandizi wako.
Kodi mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse?
Olamulira ako a mʼmizinda yonse ali kuti,
amene iwe unanena za iwo kuti,
‘Patseni mfumu ndi akalonga?’
Choncho Ine ndinakupatsani mfumu mwachipseramtima,
ndipo ndinayichotsa mwaukali.
Kulakwa kwa Efereimu kwasungidwa,
machimo ake alembedwa mʼbuku.
Zowawa zonga za mayi pa nthawi yobala mwana zamugwera,
koma iye ndi mwana wopanda nzeru,
pamene nthawi yake yobadwa yafika
iyeyo safuna kutuluka mʼmimba mwa amayi ake.
“Ndidzawapulumutsa ku mphamvu ya manda;
ndidzawawombola ku imfa.
Kodi iwe imfa, miliri yako ili kuti?
Kodi iwe manda, kuwononga kwako kuli kuti?
“Sindidzachitanso chifundo,
ngakhale Efereimu akondwe pakati pa abale ake,
mphepo ya kummawa yochokera kwa Yehova idzabwera,
ikuwomba kuchokera ku chipululu.
Kasupe wake adzaphwa
ndipo chitsime chake chidzawuma.
Chuma chake chonse chamtengowapatali
chidzafunkhidwa ndipo chidzatengedwa.
Anthu a ku Samariya adzalangidwa chifukwa cha zolakwa zawo,
chifukwa anawukira Mulungu wawo.
Adzaphedwa ndi lupanga;
ana awo adzaphedwa mowamenyetsa pansi,
akazi awo oyembekezera adzatumbulidwa pa mimba.”
Kulapa Kubweretsa Madalitso
Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.
Machimo anu ndi amene akugwetsani!
Bweretsani zopempha zanu
ndipo bwererani kwa Yehova.
Munene kwa Iye kuti,
“Tikhululukireni machimo athu onse
ndi kutilandira mokoma mtima,
kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
Asiriya sangatipulumutse;
ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,
sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’
kwa zimene manja athu omwe anazipanga,
pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”
Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo
ndipo ndidzawakonda mwaufulu
pakuti ndaleka kuwakwiyira.
Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli
Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.
Adzazika mizu yake pansi
ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
mphukira zake zidzakula.
Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,
kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.
Iye adzakula bwino ngati tirigu.
Adzachita maluwa ngati mphesa
ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?
Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.
Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;
zipatso zako zimachokera kwa Ine.”
Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.
Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.
Njira za Yehova ndi zolungama;
anthu olungama amayenda mʼmenemo,
koma anthu owukira amapunthwamo.