- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
HAGAI
Hagai
Hagai
Hag
Hagai
Za Kumanga Nyumba ya Yehova
Chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo, tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chimodzi, Yehova anapatsa mneneri Hagai uthenga wopita kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, ndiponso kwa mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki:
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Anthu awa amanena kuti, ‘Nthawi sinafike yoti nʼkumanga Nyumba ya Yehova.’ ”
Tsono Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti, “Kodi ino ndi nthawi yoti inuyo muzikhala mʼnyumba zomanga bwino, pamene Nyumba yangayi ikanali bwinja?”
Tsono zimene Yehova Wamphamvuzonse akunena ndi izi, “Ganizirani bwino njira zanu. Mwadzala zambiri, koma mwakolola zochepa. Mumadya, koma simukhuta. Mumamwa, koma ludzu lanu silitha. Mumavala, koma simumva kutentha. Mumalandira malipiro, koma ndalama zanu zimatha ngati mwaziyika mʼthumba lobowoka.”
Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Ganizirani bwino njira zanu. Pitani ku mapiri ndipo mukatenge matabwa oti mudzamangire Nyumba yanga, kuti ndikondwere nayo ndi kulandiramo ulemu,” akutero Yehova. “Mumayembekezera zambiri, koma taonani mwapeza pangʼono pokha. Zimene munazibweretsa ku nyumba, Ine ndinazimwaza. Nʼchifukwa chiyani?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. “Chifukwa Nyumba yanga ikanali bwinja, pamene aliyense wa inu watanganidwa kumanga nyumba yake. Choncho, chifukwa cha inu, mitambo yaleka kugwetsa mvula ndipo dziko lapansi laleka kutulutsa zomera. Ndabweretsa chilala pa minda ndi pa mapiri, chilala chawumitsa tirigu, mphesa, mafuta a olivi ndi chilichonse chimene chimamera pa nthaka, pa anthu ndi pa ngʼombe, ndi pa ntchito zonse za manja anu.”
Pamenepo Zerubabeli mwana wa Sealatieli, mkulu wa ansembe Yoswa mwana wa Yehozadaki, ndi anthu onse otsala anamvera mawu a Yehova Mulungu wawo ndi uthenga wa Hagai, chifukwa anatumidwa ndi Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthuwo anaopa Yehova.
Tsono Hagai, mthenga wa Yehova, anapereka kwa anthuwo uthenga uwu wa Yehova: “Ine ndili nanu,” akutero Yehova. Kotero Yehova anakhudza mtima wa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, mtima wa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndiponso mitima ya anthu onse otsala. Iwo anabwera ndi kuyamba ntchito yomanga Nyumba ya Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wawo, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chimodzi, wa chaka chachiwiri cha Mfumu Dariyo.
Ulemerero wa Nyumba Yatsopano ya Yehova
Pa tsiku la 21 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, Yehova anayankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti: “Yankhula kwa Zerubabeli mwana wa Sealatieli, bwanamkubwa wa Yuda, kwa Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe, ndi kwa anthu onse otsala. Afunse kuti, ‘Kodi alipo amene watsala pakati panu amene anaona ulemerero wakale wa Nyumba iyi? Nanga tsopano ikuoneka motani kwa inu? Kodi sikuoneka ngati yopanda pake kwa inu? Iwe Zerubabeli, limba mtima tsopano,’ akutero Yehova. ‘Limba mtima, iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki, mkulu wa ansembe. Limbani mtima, anthu nonse a mʼdziko,’ akutero Yehova, ‘ndipo gwirani ntchito. Pakuti ine ndili nanu,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Izi ndi zimene ndinapangana nanu pamene munkatuluka ku Igupto. Ndipo Mzimu wanga uli pakati panu. Musachite mantha.’
“Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakapita nthawi pangʼono ndidzagwedezanso thambo ndi dziko lapansi, nyanja ndi mtunda. Ndidzagwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo chimene mitundu yonse ya anthu imachifuna chidzabwera, ndipo ndidzaza Nyumba ino ndi ulemerero,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Siliva yense ndi wanga, golide yense ndi wanganso,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ulemerero wa nyumba iyi udzaposa ulemerero wa nyumba yoyamba ija,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse. ‘Ndipo pamalo pano ndidzakhazikitsapo mtendere,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”
Madalitso kwa Anthu Oyipitsidwa
Chaka chachiwiri cha Dariyo, pa tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi, Yehova anayankhula ndi mneneri Hagai kuti: “Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Funsa ansembe za zimene lamulo likunena: Ngati munthu wakulunga nyama yopatulika mu mkanjo wake, ndipo mkanjowo nʼkukhudza buledi kapena msuzi, kapena vinyo, mafuta kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse, kodi zimenezo zimasanduka zopatulika?’ ”
Ansembe anayankha kuti, “Ayi.”
Pamenepo Hagai anati, “Ngati munthu amene anayipitsidwa pokhudza mtembo akhudza chimodzi cha zinthu zimenezi, kodi chinthucho chimayipitsidwa?”
Ansembe anayankha kuti, “Inde, chimayipitsidwa.”
Pamenepo Hagai anati, “ ‘Ndi mmene zilili ndi anthu awa ndi dziko ili pamaso panga,’ akutero Yehova. ‘Chilichonse amachita ndiponso chilichonse chimene amapereka nʼchodetsedwa.
“ ‘Tsopano muganizire zimenezi kuyambira lero mpaka mʼtsogolo. Ganizirani momwe zinthu zinalili asanayambe kumanga nyumba ya Yehova. Pamene munthu ankayembekezera miyeso ya tirigu makumi awiri ankangopeza khumi yokha. Munthu akapita kuti akatunge miyeso makumi asanu ya vinyo mu mtsuko, ankangopeza miyeso makumi awiri yokha. Ndinawononga ntchito yonse ya manja anu ndi chinsikwi, chiwawu ndi matalala, komabe inu simunatembenukire kwa Ine,’ akutero Yehova ‘Kuyambira lero tsiku la 24 la mwezi wachisanu ndi chinayi mpaka mʼtsogolo, chonde ganizirani bwino tsiku limene munayika maziko a nyumba ya Yehova. Ganizirani bwino. Kodi mʼnkhokwe mwatsala mbewu? Mpaka lero, mpesa ndi mtengo wa mkuyu, makangadza ndi mtengo wa olivi sizinabereke zipatso.
“ ‘Kuyambira lero mpaka mʼtsogolo ndidzakudalitsani.’ ”
Zerubabeli Mphete Yolamulira ya Yehova
Yehova anayankhula ndi Hagai kachiwiri, pa tsiku la 24 la mwezi kuti: “Uza Zerubabeli, bwanamkubwa wa Yuda, kuti ndidzagwedeza thambo ndi dziko lapansi. Ndidzagwetsa mipando yaufumu ndi kuwononga mphamvu za maufumu achilendo. Ndidzagubuduza magaleta ndi okwerapo ake; akavalo ndi okwerapo ake adzagwa, aliyense adzaphedwa ndi lupanga la mʼbale wake.
“ ‘Tsiku limenelo,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse, ‘ndidzakutenga, iwe mtumiki wanga Zerubabeli mwana wa Sealatieli,’ akutero Yehova, ‘ndipo ndidzakusandutsa kukhala mphete yanga yolamulira, pakuti ndasankha iwe,’ akutero Yehova Wamphamvuzonse.”