- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
EZEKIELI
Ezekieli
Ezekieli
Ezek
Ezekieli
Zolengedwa za Moyo ndi Ulemerero wa Yehova
Tsiku lachisanu la mwezi wachinayi, chaka cha makumi atatu, ine ndinali pakati pa amʼndende mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara. Tsono kumwamba kunatsekuka ndipo ndinaona maonekedwe a Mulungu mʼmasomphenya.
Pa tsiku lachisanu la mwezi, chaka chachisanu Yehoyakini ali mʼndende, Yehova anayankhula ndi wansembe Ezekieli, mwana wa Buzi, mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara mʼdziko la Ababuloni. Dzanja la Yehova linali pa iye kumeneko.
Ndinayangʼana ndipo ndinangoona mphepo yamkuntho ikubwera kuchokera kumpoto. Panali mtambo waukulu wozunguliridwa ndi kuwala ndipo moto unali lawilawi kuchokera mu mtambowo. Pakati pa motowo pankaoneka ngati mkuwa wonyezimira. Mʼkatikati mwa motowo munali zinthu zinayi zamaonekedwe a nyama. Thupi lawo limaoneka ngati la munthu koma chilichonse chinali ndi nkhope zinayi ndiponso mapiko anayi. Miyendo yake inali yowongoka; mapazi ake anali a ziboda ngati phazi la mwana wangʼombe. Ndipo zibodazo zinkawala ngati mkuwa wonyezimira. Mʼmunsi mwa mapiko awo kumbali zonse zinayi, nyamazo zinali ndi manja a munthu. Zonse zinayi zinali ndi nkhope ndi mapiko, ndipo mapiko awowo anakhudzana. Chilichonse chimapita molunjika kutsogolo; sizimatembenuka pamene zimayenda.
Nkhope zawo zimaoneka motere: Chilichonse chinali ndi nkhope ya munthu, ndipo mbali ya kumanja chilichonse chinali ndi nkhope zinayi zosiyana motere: nkhope ya munthu, nkhope ya mkango ku dzanja lamanja, nkhope ya ngʼombe ku dzanja lamanzere, ndipo kumbuyo kwake nkhope ya chiwombankhanga. Ndi mʼmene zinalili nkhope zawo. Mapiko awo anali otambasukira mmwamba. Chamoyo chilichonse chinali ndi mapiko awiri okhudzana ndi mapiko a chinzake. Chinalinso ndi mapiko ena awiri ophimbira thupi lake. Zamoyozo zinkayenda molunjika kutsogolo. Kulikonse kumene mzimu umazitsogolera kupita, nazonso zimapita kumeneko, osatembenuka pamene zikupita. Pakati pa zamayozo panali chinthu chooneka ngati makala oyaka kapena miyuni yoyaka. Moto umayendayenda pakati pa zamayozo; wowala kwambiri, ndipo mphenzi zimatuluka pakati pawo. Zamoyozo zinkathamanga uku ndi uko ngati kungʼanima kwa mphenzi.
Pamene ndinali kuyangʼana zamoyozo, ndinangoona mikombero ndipo pansi pambali pa chamoyo chilichonse panali mkombero umodzi. Maonekedwe a mikomberoyo anali ngati mwala wonyezimira. Mikombero yonse inali yofanana ndipo mapangidwe awo anali ngati wongolowanalowana. Mikombero ija poyenda inkatha kupita mbali iliyonse yomwe zamoyozo zinayangʼana popanda kutembenuka. Marimu a mikomberoyo anali aatali ndi ochititsa mantha ndipo marimu onse anayi anali ndi maso ponseponse.
Zamoyozo zinkati zikamayenda, mikomberoyo imayendanso mʼmbali mwake; ndipo zamoyozo zinkati zikamakwera mmwamba, mikomberoyo imakweranso. Kulikonse kumene mzimu wake unkazitsogolera, zamoyozo zinkapita komweko. Ndipo mikombero ija inkapita nawo pamodzi popeza kuti mzimu wa zamoyozo ndiwo umayendetsa mikombero ija. Zamoyo zija zinkati zikamayenda mikombero imayendanso. Zamoyozo zimati zikayima, nayonso mikombero inkayima. Zamoyozo zinkati zikawuluka, mikomberonso imawuluka nazo pamodzi chifukwa mzimu wa zamoyo zija ndiwo umayendetsa mikombero ija.
Pamwamba pa mitu ya zamoyozo panali chinthu chonga thambo, lowala ndipo kunyezimira kwake ngati galasi loyangʼanitsa ku dzuwa, loyalidwa pamwamba pa mitu yake. Zamoyozo zinatambalitsa mapiko ake mʼmunsi mwa thambo lija, mapiko ake ena kumakhudzana, mapiko awiri kumaphimba thupi lake. Pamene zamoyo zimayenda ndimamva phokoso la mapiko ake, ngati mkokomo wa madzi ambiri, ngati liwu la Wamphamvuzonse, ngati phokoso la gulu lankhondo. Zimati zikayima zinkagwetsa mapiko ake.
Ndipo panamveka mawu kuchokera pamwamba pa thambo la pa mitu ya zamoyo zija. Nthawi iyi nʼkuti zamoyozo zitayima ndi kugwetsa pansi mapiko ake. Pamwamba pa thambo la pa mitu yake panali chinthu chimene chimaoneka ngati mpando waufumu wopangidwa ndi mwala wa safiro, ndipo pamwamba pa mpando waufumuwo panali chinthu chooneka ngati munthu. Ndinaona kuti mmwamba mwa chiwuno chake munali ngati chitsulo chowala konsekonse ngati moto. Mʼmunsi mwa chiwuno chake munalinso ngati moto wokhawokha. Kuwala kwa mphamvu kunamuzungulira munthuyo. Kuwalako kunali ndi maonekedwe a utawaleza mʼmitambo tsiku limene kwagwa mvula.
Umu ndi mmene ulemerero wa Yehova umaonekera. Pamene ndinawuona ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akundiyankhula.
Kuyitanidwa kwa Ezekieli
Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, imirira kuti ndiyankhule nawe.” Pamene ankayankhula nane, Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa, ndipo ndinamva Iye akundiyankhula.
Iye anati, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikukutuma kwa Aisraeli, mtundu wa anthu owukira umene wandiwukira Ine; Iwo ndi makolo awo akhala akundiwukira Ine mpaka lero lino. Ndikukutuma kwa anthu okanika ndiponso nkhutukumve. Ndikukutuma kuti akawawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena. Kaya akamva kaya sakamvera, pakuti iwo ndi anthu opanduka, komabe adzadziwa kuti mneneri ali pakati pawo. Tsono iwe mwana wa munthu, usachite nawo mantha kapena kuopa zimene azikanena. Usachite mantha, ngakhale minga ndi mkandankhuku zikuzinge ndipo ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena kapena kuopsedwa ndi nkhope zawo, popeza anthuwa ndi awupandu. Ukawawuze ndithu mawu anga, kaya akamva kaya sakamva. Paja anthuwa ndi awupandu. Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuwuza. Usakhale wowukira ngati iwowo. Tsono yasama pakamwa pako kuti udye chimene ndikukupatsa.”
Nditayangʼana ndinangoona dzanja litaloza ine, litagwira mpukutu wolembedwa. Anawufunyulura pamaso panga. Mpukutu wonse unali wolembedwa kuseri nʼkuseri. Ndipo mawu amene analembedwa mʼmenemo anali a madandawulo, maliro ndi matemberero.
Tsono Mulungu anandiwuza kuti, “Mwana wa munthu, idya chimene ndikukupatsachi. Idya kenaka upite ukayankhule ndi Aisraeli.” Choncho ndinayasama ndipo anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.
Kenaka Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsa kuti ukhute.” Choncho ndinadya, ndipo unkatsekemera ngati uchi mʼkamwa mwanga.
Pamenepo Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, pita tsopano kwa Aisraeli ndipo ukawawuze mawu anga. Sindikukutuma kwa anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, koma kwa Aisraeli. Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu oyankhula chiyankhulo chachilendo ndi chovuta, amene mawu ake sungawamvetse. Ndithu ndikanakutuma kwa iwowa, bwenzi iwo atakumvera. Koma Aisraeli sadzakumvera chifukwa iwo sakufuna kumvera Ine. Paja Aisraeli onse ndi okanika ndiponso a mtima wowuma. Tsono ine ndakhwimitsa nkhope yako mofanana ndi nkhope zawo. Ndalimbitsanso mutu wako mofanana ndi mitu yawo. Ine ndidzakusandutsa wolimba ngati mwala wa dayimondi umene uposa thanthwe lina lililonse kulimba kwake. Usachite nawo mantha kapena kuopsedwa nawo. Paja anthuwa ndi awupandu.”
Anatinso, “Iwe mwana wa munthu, umvetsetse bwino zimene ndikukuwuzazi ndipo mawu angawa uwasunge bwino mu mtima mwako. Tsopano upite kwa Aisraeli anzako amene ali ku ukapolo ndipo ukayankhule nawo. ‘Kaya akamvera kaya sakamvera,’ koma uzikawawuza kuti, Ambuye Wamphamvuzonse akuti zakutizakuti.”
Pamenepo Mzimu unandinyamula ndipo kumbuyo kwanga ndinamva liwu lamphamvu ngati chivomerezi chachikulu, lonena kuti, “Utamandike ulemerero wa Yehova kumene Iye amakhala!” Phokoso ndinkalimvalo linali la kugundana kwa mapiko a zamoyo ndiponso phokoso la mikombero ya pambali pake ija, limene linkamveka ngati chivomerezi chachikulu. Mzimu wa Yehova unandikweza ndi kundinyamula ndipo ndinachokapo ndili wowawidwa ndi wonyuka mu mtima. Ndipo dzanja la Yehova linali pa ine mwa mphamvu. Choncho ndinafika kwa amene anali mu ukapolo ku Telabibu pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Ndinakhala pansi pakati pawo masiku asanu ndi awiri, ndili wothedwa nzeru kwambiri.
Chenjezo kwa Israeli
Atatha masiku asanu ndi awiriwo, Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ine ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Uziti ukamva mawu anga, ndiye uzikawachenjeza. Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe udzafa ndithu,’ koma iwe osamuchenjeza kapena kumuyankhula kuti aleke njira zake zoyipa ndi kuti akhale ndi moyo, munthu woyipayo adzafa mu uchimo wake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma ukamuchenjeza munthu woyipa koma iye osatembenuka mtima kuleka zoyipa zake kapena kusiya njira zake zoyipa, munthuyo adzafa chifukwa cha uchimo wake koma iwe udzapulumutsa moyo wako.
“Ngati munthu wolungama asiya chilungamo chake ndi kuchita uchimo ndipo Ine nʼkumuyika mʼzoopsa, munthuyo adzafa ndithu. Popeza iwe sunamuchenjeze, adzafadi chifukwa cha tchimo ndipo chilungamo chake sichidzakumbukiridwa, koma ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma ngati umuchenjeza munthu wolungama kuti asachimwe ndipo iye nʼkuleka kuchimwa adzakhala ndi moyo ndithu chifukwa anamvera chenjezo, ndipo iwe udzapulumutsa moyo wako.”
Nthawi ina dzanja la Yehova linali pa ine ndipo anandiwuza kuti, “Nyamuka upite ku chigwa, kumeneko ndikayankhula nawe.” Choncho ndinanyamuka kupita ku chigwa. Ndipo ndinaona ulemerero wa Yehova kumeneko, ngati ulemerero umene ndinaona mʼmbali mwa mtsinje wa Kebara ndipo ndinagwa pansi chafufumimba.
Koma Mzimu wa Mulungu unalowa mwa ine ndipo unandiyimiritsa. Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Pita, kadzitsekere mʼnyumba mwako. Ndipo iwe mwana wa munthu, adzakumanga ndi zingwe motero kuti sudzatha kuyendanso pakati pa anthu. Ndidzamatirira lilime lako kukhosi, kotero kuti udzakhala chete wosatha kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu aupandu. Koma pamene ndidzayankhula kwa iwe, ndidzatsekula pakamwa pako ndipo udzawawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti zakutizakuti.’ Aliyense wofuna kumva amve ndipo wokana kumva, muleke akane; pakuti iwo ndi anthu opanduka.”
Chionetsero cha Kuzingidwa kwa Yerusalemu
Mulungu anati, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga njerwa, uliyike pamaso pako ndipo ujambulepo chithunzi cha mzinda wa Yerusalemu. Ndipo uwuzinge mzindawo motere: uwumangire nsanja zowuzinga, uwumbire mitumbira ya nkhondo, uwumangire misasa ya nkhondo ndipo uyike zida zogumulira kuzungulira mzindawo. Kenaka utenge chiwaya chachitsulo uchiyike ngati khoma lachitsulo pakati pa iwe ndi mzindawo. Uyangʼanitsitse mzindawo ndipo udzakhala wozingidwa ndi nsanja za nkhondo. Choncho umangire nsanja zankhondo. Chimenechi chidzakhala chizindikiro kwa Aisraeli.
“Tsono iwe ugonere kumanzere kwako ndipo ndidzayika pa iwe tchimo la Aisraeli. Iwe udzasenza tchimolo masiku onse amene udzagonere mbali imeneyo. Ine ndakuyikira masiku okwana 390 malingana ndi zaka za machimo awo. Umu ndi mmene udzasenzere machimo a Aisraeli.
“Utatha zimenezo udzagonerenso mbali ya kudzanja lamanja, ndipo udzasenza machimo a anthu a ku Yuda masiku makumi anayi, tsiku lililonse kuyimira chaka chimodzi. Tsono udzayangʼanitsitse nsanja za nkhondo zozinga. Dzanja la mkanjo wako utalikwinya ndi dzanja lako utakweza, udzalosere modzudzula Yerusalemu. Ine ndidzakumanga ndi zingwe kotero kuti sudzatha kutembenukira uku ndi uku mpaka utatsiriza masiku akuzingidwa ako.
“Tsono tenga tirigu ndi barele, nyemba ndi mphodza, mapira ndi mchewere; ndipo uyike zonsezi mʼmbale imodzi ndipo upange buledi wako. Uzidya pa masiku 390 amene udzakhala ukugonera mbali imodzi. Uyeze theka la kilogalamu la chakudyacho kuti uzidya tsiku lililonse kamodzi kokha. Uyezenso zikho ziwiri zamadzi ndipo uzimwa tsiku ndi tsiku. Uzidya chakudya chako ngati momwe amadyera keke ya barele. Uzidzaphika chakudyacho anthu akuona pogwiritsa ntchito ndowe ya munthu ngati nkhuni.” Yehova anati, “Chimodzimodzi anthu a Israeli adzadya chakudya chodetsedwa ku mayiko achilendo kumene Ine ndidzawapirikitsira.”
Koma ine ndinati, “Zisatero, Ambuye Yehova! Ine sindinadziyipitsepo pa zachipembedzo. Kuyambira ubwana wanga mpaka tsopano, sindinadyepo kanthu kalikonse kopezeka katafa kapena kophedwa ndi zirombo za kutchire. Palibe nyama yodetsedwa pa zachipembedzo imene inalowa pakamwa panga.”
Iye anati, “Chabwino, ndidzakulola kuti uphike buledi wako ndi ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa ndowe za munthu.”
Pambuyo pake anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Yerusalemu ndidzawachepetsera chakudya. Anthuwo adzadya chakudya chochita kuyeza ndipo azidzadya mwa nkhawa. Azidzamwanso madzi ochita kuyeza ndiponso mwa mantha. Ndidzachita zimenezi kuti adzasowe chakudya ndi madzi. Choncho adzachita nkhawa akumapenyana ndipo adzatheratu ndi kuwonda chifukwa cha machimo awo.”
Chizindikiro cha Chiweruzo
Tsiku lina Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano tenga lupanga lakuthwa ndipo uligwiritse ntchito ngati lumo lometera. Umete tsitsi ndi ndevu zako. Kenaka utenge sikelo ndipo ugawe tsitsilo patatu. Kuzinga mzinda kuja kukatha, chimodzi cha zigawo zitatu za tsitsilo uchitenthe pakati pa mzinda. Chigawo chachiwiri uchiduledule ndi lupanga, poyenda muzungulire mzinda wonsewo. Chigawo chachitatu uchimwazire ku mphepo, ndidzachitsata nditasolola lupanga. Koma utengeko tsitsi pangʼono, ulimange mu mpindiro wa mkanjo wako. Pa tsitsi limeneli utapepo lina, uliponye pa moto ndi kulitentha. Moto udzayambira pamenepo mpaka ku nyumba yonse ya Israeli.”
Ambuye Yehova akunena kuti, “Uyu ndi Yerusalemu amene ndamuyika pakati pa mitundu ya anthu, ndipo mayiko onse amuzungulira. Koma anthu a Yerusalemu aphwanya malamulo anga pochita zoyipa kuposa anthu a mitundu ina. Iwo anandipandukira kupambana anthu ena amene awazungulira. Iwo anakana malamulo anga ndipo sanasunge malangizo anga.
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Popeza mwakhala osamvera kupambana anthu a mitundu ina amene akuzungulirani, popeza simunatsate malamulo anga kapena kusunga malangizo anga, mʼmalo mwake mwakhala mukutsata makhalidwe a anthu a mitundu ina amene akuzungulirani.
“Tsono Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndikutsutsana nawe, Yerusalemu, choncho Ine ndidzakulangani. Ine ndidzakulangani anthu a mitundu ina akuona. Chifukwa cha ntchito zanu zonyansa ndidzakulangani ndi chilango chimene sindinakulangeni nacho nʼkale lomwe ndipo sindidzakulangani ndi chofanana nacho mʼtsogolomo. Tsono pakati panu makolo adzadya ana awo, ndipo ana adzadya makolo awo. Ndidzakulanga ndipo otsala onse ndidzawabalalitsa ku mphepo zonse zinayi. Ndithu, pali Ine, akutero Ambuye Yehova Wamoyo, pakuti mwayipitsa Nyumba yanga ndi mafano ano oyipa ndi miyambo yanu yonyansa, Inenso ndidzakulangani. Sindidzakulekererani kapena kukumverani chisoni. Chimodzi mwa zigawo zitatu za anthu ako chidzafa ndi mliri, kapena chidzawonongeka ndi njala; chigawo china chidzaphedwa ndi lupanga kunja kwa mzinda, ndipo chigawo china ndidzachibalalitsira ku mphepo zonse zinayi pochita kuchithamangitsa.
“Ndi mmene udzachitire mkwiyo wanga. Ndikadzatsiriza kuwalanga, pamenepo mtima wanga udzakhala pansi. Adzadziwa kuti Ine Yehova ndinawayankhula mwa nsanje ndikadzawalanga.
“Ndidzakusandutsa iwe bwinja ndi chinthu chonyozeka pakati pa anthu a mitundu ina amene akuzungulira, ndi kwa onse odutsapo Udzakhala chinthu chonyozeka ndi chonyogodoledwa. Udzakhala chenjezo ndi chinthu choopsa kwa anthu a mitundu ina amene akuzungulira ndikadzakulanga mokwiya ndi mwaukali ndi kugamula mlandu wako mokwiya. Ine Yehova ndayankhula. Pamene ndidzakulasa ndi njala yolasa ngati mivi yoopsa ndi yosakaza ndidzatero nʼcholinga choti ndikuwonongeni. Ndidzagwetsa njalayo pa iwe mowirikiza pochepetsa chakudya chako cha tsiku ndi tsiku. Ndidzatumiza njala ndi zirombo za kuthengo, ndipo zidzakulanda ana ako. Mliri ndi kuphana zidzakhala pakati pako, ndipo ndidzakubweretsera nkhondo. Ine Yehova ndayankhula.”
Uneneri Wotsutsa Mapiri a Israeli
Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku mapiri a Israeli; yankhula nawo modzudzula kuti, ‘Inu mapiri a ku Israeli, imvani mawu a Ambuye Yehova. Iye akuwuza mapiri, magomo, mitsinje ndi zigwa kuti: Ine ndizakuthirani nkhondo ndipo ndidzawononga nyumba zanu mʼmene mukupembedzeramo mafano. Maguwa anu ansembe adzagumulidwa ndipo maguwa anu ofukizira lubani adzaphwanyidwa; ndipo ndidzapha anthu anu pamaso pa mafano anu. Ine ndidzagoneka mitembo ya Aisraeli pamaso pa mafano awo, ndipo ndidzamwaza mafupa anu mozungulira maguwa anu ansembe. Konse kumene mumakhala, mizinda yanu idzasanduka bwinja. Nyumba zanu zopembedzera mafano zidzagumulidwa kotero kuti maguwa anu adzawonongedwa ndi kusakazidwa, mafano anu adzaphwanyidwa ndi kuwonongedwa. Maguwa anu ofukizirapo lubani adzagwetsedwa pansi ndipo zonse zimene munapanga zidzatheratu. Anthu anu adzaphedwa pakati panu, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’
“Komabe ndidzasiya ena pangʼono opulumuka ku nkhondo. Iwowa ndidzawamwazira ku mayiko ena pakati pa anthu a mitundu ina. Pamenepo opulumuka mwa inu adzandikumbukira ku mayiko kumene anatengedwa ukapolo. Ndidzawamvetsa chisoni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo ndi kundipandukira kuja ndiponso chifukwa kuti anayika mtima wawo pa mafano. Choncho adzachita okha manyazi chifukwa cha zoyipa zimene ankachita ndi miyambo yonyansa imene ankatsata. Ndipo iwo adzadziwa kuti ndine Yehova ndi kuti sindinkawaopseza chabe pamene ndinanena kuti ndidzawawononga.
“Ambuye Yehova akuti: Womba mʼmanja mwako ndipo uponde mapazi ako pansi mwamphamvu ndipo ufuwule kuti, ‘Mayo!’ chifukwa cha zonyansa ndi zoyipa zonse zimene Aisraeli achita, pakuti adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri. Amene ali kutali adzafa ndi mliri, ndipo amene ali pafupi adzafa pa nkhondo, ndipo amene adzapulumuke ndi kusaphedwa adzafa ndi njala. Kotero ndidzakwaniritsa ukali wanga pa iwo. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene anthu awo adzagona atafa pakati pa mafano awo mozungulira maguwa awo ansembe, pamwamba pa magomo ndi mapiri onse, pansi pa mtengo uliwonse watambalala ndi wa thundu uliwonse wamasamba ambiri, kumalo kumene ankapereka nsembe zonunkhira kwa mafano awo onse. Choncho ndidzawalanga ndi mkono wanga ndi kusandutsa dziko kukhala bwinja. Dziko lonse kumene akukhala kuyambira ku chipululu mpaka ku mzinda wa Ribula ndidzalisandutsa bwinja. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chimaliziro Chafika
Yehova anandipatsa uthenga uwu kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuwuza dziko la Israeli kuti:
“Chimaliziro! Chimaliziro chafika
ku ngodya zinayi za dziko.
Chimaliziro chili pa iwe tsopano.
Mkwiyo wanga ndidzawuthira pa iwe.
Ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndi kukulanga chifukwa cha zonyansa zako.
Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga ndithu chifukwa cha ntchito zako zoyipa
komanso chifukwa cha miyambo yako yonyansa imene ili pakati pako.
Pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
“Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi:
“Chiwonongeko! Chiwonongeko chimene sichinamvekepo!
Taona chikubwera!
Chimaliziro chafika!
Chimaliziro chafika!
Chiwonongeko chakugwera.
Taona chafika!
Inu anthu okhala mʼdziko,
chiwonongeko chakugwerani.
Nthawi yafika, tsiku layandikira; tsiku la chisokonezo osati la chimwemwe pa mapiri.
Ine ndili pafupi kukukwiyirani,
ndipo ukali wanga udzathera pa iwe;
Ine ndidzakuweruza molingana ndi machitidwe ako
ndiponso ndidzakulanga chifukwa cha miyambo yako yonyansa.
Ine sindidzakumvera chisoni
kapena kukuleka.
Ndidzakulanga malingana ndi ntchito zako
ndiponso chifukwa cha miyambo yako yonyansa pakati pako.
‘Pamenepo udzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndimakantha.’
“Taona, tsikulo!
Taona, lafika!
Chiwonongeko chako chabwera.
Ndodo yaphuka mphundu za maluwa.
Kudzitama kwaphuka.
Chiwawa chasanduka ndodo
yowakwapulira chifukwa cha kuyipa kwawo.
Palibe mwa anthu amenewo amene adzatsale.
Palibe ndi mmodzi yemwe mwa unyinji wawo.
Palibiretu ndipo sipadzapezeka
munthu wowalira maliro.
Nthawi yafika!
Tsiku layandikira!
Munthu wogula asakondwere
ndipo wogulitsa asamve chisoni,
popeza ukali wanga uli pa gulu lonse.
Wogulitsa sadzazipezanso zinthu
zimene anagulitsa kwa wina
chinkana onse awiri akanali ndi moyo,
pakuti chilango chidzagwera onsewo
ndipo sichingasinthike.
Chifukwa cha machimo awo, palibe aliyense
amene adzapulumutsa moyo wake.
“Lipenga lalira,
ndipo zonse zakonzeka.
Koma palibe ndi mmodzi yemwe amene akupita ku nkhondo,
pakuti mkwiyo wanga uli pa gulu lonse.
Ku bwalo kuli kumenyana
ndipo mʼkati muli mliri ndi njala.
Anthu okhala ku midzi
adzafa ndi nkhondo.
Iwo okhala ku mizinda
adzafa ndi mliri ndi njala.
Onse amene adzapulumuka
ndi kumakakhala ku mapiri,
azidzalira ngati nkhunda za ku zigwa.
Aliyense azidzabuwula chifukwa cha machimo ake.
Dzanja lililonse lidzalefuka,
ndipo bondo lililonse lidzalobodoka ngati madzi.
Iwo adzavala ziguduli
ndipo adzagwidwa ndi mantha.
Adzakhala ndi nkhope zamanyazi
ndipo mitu yawo adzameta mpala.
“Iwo adzataya siliva wawo mʼmisewu
ndipo golide wawo adzakhala chinthu chonyansa.
Siliva ndi golide wawo
sizidzatha kuwapulumutsa
pa tsiku la ukali wa Yehova.
Chuma chawochi sichidzawathandiza kuthetsa njala,
kapena kukhala okhuta,
pakuti ndicho chinawagwetsa mʼmachimo.
Iwo ankanyadira zodzikongoletsera zawo zamakaka
ndipo ankazigwiritsa ntchito kupanga mafano awo onyansa ndi zonyansa zawo zina.
Nʼchifukwa chake Ine ndidzazisandutsa
kukhala zowanyansa.
Ndidzazipereka kwa alendo kuti azifunkhe.
Anthu oyipa a dziko lapansi adzazilanda
ndi kudziyipitsa.
Ine ndidzawalekerera anthuwo
ndipo adzayipitsa malo anga apamtima.
Adzalowamo ngati mbala
ndi kuyipitsamo.
“Konzani maunyolo,
chifukwa dziko ladzaza ndi anthu opha anzawo
ndipo mzinda wadzaza ndi chiwawa.
Ndidzabweretsa mitundu ya anthu oyipitsitsa
kuti idzalande nyumba zawo.
Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu
pamene anthu akunja adzalowa mʼmalo awo achipembedzo ndi kuyipitsamo.
Nkhawa ikadzawafikira
adzafunafuna mtendere koma osawupeza.
Tsoka lidzatsatana ndi tsoka linzake,
ndipo mphekesera idzatsatana ndi mphekesera inzake.
Iwo adzayesa kufuna masomphenya kuchokera kwa mneneri.
Adzasowa ansembe owaphunzitsa malamulo,
ndipo anthu akuluakulu sadzakhalanso ndi uphungu.
Mfumu idzalira,
kalonga adzagwidwa ndi mantha.
Manja a anthu a mʼdzikomo azidzangonjenjemera ndi mantha.
Ine ndidzawalanga molingana ndi machitidwe awo,
ndipo ndidzawaweruza molingana ndi momwe anaweruzira anzawo.
Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Kupembedza Mafano Mʼnyumba ya Mulungu
Tsiku lachisanu la mwezi wachisanu ndi chimodzi, mʼchaka chachisanu ndi chimodzi, ndinakhala mʼnyumba mwanga pamodzi ndi akuluakulu a ku Yuda. Tsono mphamvu za Ambuye Yehova zinandifikira. Nditayangʼana ndinangoona chinthu chooneka ngati munthu. Kuchokera pamene pamaoneka ngati chiwuno chake kumatsika mʼmunsi anali ngati moto, ndipo kuchokera mʼchiwuno kukwera mmwamba amaoneka mowala ngati mkuwa wonyezimira. Iye anatambasula chinthu chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi la pamutu panga. Nthawi yomweyo Mzimu unandikweza mlengalenga. Tsono ndikumachita ngati ndikuona Mulungu kutulo, Mzimu uja unapita nane ku Yerusalemu nundiyika pa khomo la chipata chamʼkati choyangʼana kumpoto. Kumeneko kunali fano limene limaputa mkwiyo wa Mulungu. Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ngati momwe ndinaonera mʼmasomphenya mʼchigwa muja.
Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tayangʼana kumpoto.” Choncho ndinayangʼana kumpoto ndipo ndinaona pa khomo la chipata pafupi ndi guwa lansembe ndinaona fano loputa mkwiyo wa Mulungu lija.
Ndipo Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimene akuchitazi, zonyansa zazikulu zimene Aisraeli akuchita kuno, zinthu zondichotsa Ine kumalo anga opatulika? Koma iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri.”
Kenaka Iye anandipititsa ku khomo lolowera ku bwalo la Nyumba ya Mulungu. Nditayangʼanitsitsa ndinangoona dzenje pa khomapo. Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, tsopano bowola pa khomapo.” Ndinabowoladi pa khomapo ndipo ndinapezapo khomo.
Ndipo Yehova anandiwuza kuti, “Lowa, ndipo ona zinthu zonyansa zimene akuchita pamenepa.” Motero Ine ndinalowa ndi kuyangʼana, ndipo ndinaona pa makoma onse zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa pansi, za nyama zonyansa ndiponso za mafano onse amene Aisraeli ankapembedza. Patsogolo pa zimenezi panayima akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Aisraeli, ndipo Yaazaniya mwana wa Safani anali atayima pakati pawo. Aliyense wa iwo anali ndi chofukizira lubani mʼdzanja lake ndipo utsi wa fungo lokoma la lubani unkafuka.
Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Aisraeli akuchita mu mdima, aliyense akupembedza fano lakelake mʼnyumbamo? Iwo akuti, ‘Yehova sakutiona; Yehova walisiya dziko!’ Iye anandiwuzanso kuti, ‘Iwe udzawaonanso akuchita zinthu zonyansa kwambiri.’ ”
Kenaka anapita nane pa khomo la ku khomo la chipata cha Nyumba ya Mulungu choyangʼana kumpoto, ndipo kumeneko ndinaona akazi ena atakhala pansi, akulira mulungu wawo wotchedwa Tamuzi. Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi? Iwe udzaona zinthu zimene zili zonyansa kwambiri kuposa izi.”
Kenaka Iye anapita nane mʼkati mwa bwalo la Nyumba ya Yehova. Kumeneko ku khomo lolowera ku Nyumba ya Yehova pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna 25. Anafulatira Nyumba ya Mulungu wa Yehova ndipo nkhope zawo zinaloza kummawa, ndipo ankapembedza dzuwa choyangʼana kummawa.
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi waziona zimenezi? Kodi nʼchinthu chopepuka kuti anthu a ku Yuda azichita zonyansa zimene akuchitazi pano? Kodi afike mpaka pomafalitsa za ndewu mʼdziko lonse? Iwotu akuwutsa ukali wanga. Akundipsetsa mtima ndi zochita zawo! Choncho Ine ndidzawalanga ndili wokwiya. Sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka. Ngakhale atandifuwulira mʼmakutu mwanga sindidzawamvera.”
Opembedza Mafano Aphedwa
Pambuyo pake Yehova anandiyankhula mofuwula kuti, “Bwerani pafupi, inu odzalanga mzindawu, aliyense ali ndi chida chake mʼmanja.” Ndipo ndinaona anthu asanu ndi mmodzi akubwera kuchokera ku chipata chakumtunda chimene chimaloza kumpoto, aliyense ali ndi chida choopsa cha nkhondo mʼdzanja lake. Pagulu pawopa panali munthu wovala chovala chabafuta, atatenga zolembera pambali pake. Iwo analowa ndi kuyima pambali pa guwa lamkuwa.
Tsono ulemerero wa Mulungu wa Israeli unakwera kuchokera pamwamba pa akerubi, pamene unali, ndipo unafika pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Pamenepo Yehova anayitana munthu amene anavala chovala chabafuta uja amene anatenga zolembera pambali pake ndipo anamuwuza kuti, “Pita mu mzinda wonse wa Yerusalemu ndi kuyika chizindikiro pamphumi pa anthu amene akumva chisoni ndi kulira chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene zikuchitika mu mzindamo.”
Kenaka ndinamva Yehova akuwuza anthu ena aja kuti, “Mutsateni mu mzinda wonse ndipo mukakanthe aliyense mopanda kumvera chisoni kapena chifundo. Mukaphe kotheratu anthu okalamba, anyamata ndi atsikana, makanda ndi akazi koma musakakhudze wina aliyense amene ali ndi chizindikiro. Muyambire ku Nyumba yanga yopatulika.” Motero iwo anayamba ndi akuluakulu amene anali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
Ndipo Yehova anawawuza kuti, “Ipitsani Nyumba ya Mulungu ndipo mudzaze mabwalo ake ndi anthu akufa. Pitani.” Choncho iwo anapita nayamba kupha anthu mu mzinda monse. Pamene iwo ankapha anthu, ine ndinatsala ndekha. Tsono ndinadzigwetsa chafufumimba ndi kufuwula kuti, “Aa, Ambuye Yehova! Kodi mwawakwiyiratu anthu a ku Yerusalemu motero kuti mudzawononga kotheratu anthu onse otsala ku Israeli?”
Iye anandiyankha kuti, “Tchimo la Aisraeli ndi Yuda ndi lalikulu kwambiri; dziko ladzaza ndi zophana ndipo mu mzinda mwadzaza ndi zosalungama. Iwo akunena kuti, ‘Yehova walisiya dziko lake; Yehova sakuona.’ Choncho sindidzawamvera chisoni kapena kuwaleka, koma Ine ndidzawalanga potsata zochita zawo.”
Ndipo munthu wovala chovala chabafuta uja atatenga zolembera pambali pake anadzafotokozera Yehova kuti, “Ndachita monga munandilamulira.”
Ulemerero Uchoka ku mʼNyumba ya Mulungu
Ine nditayangʼana ku thambo limene lili pamwamba pa mitu ya akerubi ndinangoona chinthu chooneka ngati mpando waufumu wa mwala wa safiro. Tsono Yehova anawuza munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pita pakati pa mikombero kunsi kwa akerubi. Udzaze manja ako ndi makala oyaka amene ali pakati pa akerubiwo ndipo uwawaze mu mzinda.” Iye anachita zimenezi ine ndikuona.
Apa akerubiwo anali atayima mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu pamene munthuyo ankalowa. Tsono mtambo unadzaza bwalo lamʼkati. Ndipo ulemerero wa Yehova unachoka pamwamba pa akerubi ndipo unafika ku chiwundo cha Nyumba ya Mulungu. Mtambo unadzaza Nyumba ya Mulungu, ndipo kuwala kwa ulemerero wa Yehova kunadzaza bwalolo. Phokoso la mapiko a akerubi limamveka mpaka ku bwalo lakunja, monga momwe linamvekera liwu la Mulungu Wamphamvuzonse akamayankhula.
Kenaka Yehova analamula munthu wovala chovala chabafuta uja kuti, “Pala moto pakati pa mikombero, pakati pa akerubi.” Munthu uja anapitadi nakayima pa mbali pa mkombero umodzi. Ndipo mmodzi wa akerubi anatambalitsa dzanja lake mpaka pa moto umene unali pakati pawo. Iye anapalako motowo ndipo anapatsa munthu wovala chovala chabafuta uja. Tsono iye anawulandira natuluka. Ndiye kuti kunsi kwa mapiko akerubi kumaoneka zinthu zooneka ngati manja a munthu.
Ine nditayangʼanitsitsa ndinaona mikombero inayi pambali pa akerubi. Pambali pa kerubi aliyense panali mkombero umodzi; mikomberoyo inkanyezimira ngati miyala yokongola ya krizoliti. Maonekedwe a mikombero inayi ija anali ofanana. Mkombero uliwonse umaoneka ngati mkombero wolowana ndi unzake. Poyenda akerubiwo, amapita mbali iliyonse ya mbali zinayizo kumene akerubiwo amayangʼana. Mikomberoyo simatembenuka pamene akerubiwo ankayenda. Kulikonse kumene mutu walunjika nʼkumene ankapita popanda kutembenuka. Matupi awo onse, misana yawo, manja awo ndi mapiko awo zinali ndi maso okhaokha, monganso mʼmene inalili mikombero yawo inayi ija. Ine ndinamva mikombero ikutchedwa kuti, “mikombero yakamvuluvulu.” Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi. Nkhope yoyamba inali ya Kerubi, nkhope yachiwiri inali ya munthu, nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope yachinayi inali ya chiwombankhanga.
Tsono akerubi aja anawuluka. Izi zinali zamoyo zija zimene ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Pamene akerubi ankayenda, nayonso mikombero ya mʼmbali mwawo inkayenda. Akerubiwo ankati akatambasula mapiko awo kuti auluke mikombero sinkachoka mʼmbali mwawo. Akerubiwo ankati akayima, mikombero inkayimanso. Ngati akerubiwo auluka, mikomberoyo inkapita nawo chifukwa mzimu wa zamoyozo ndiwo unkayendetsa mikomberoyo.
Pamenepo ulemerero wa Yehova unachoka pa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu ndi kukakhala pamwamba pa akerubi. Ine ndikuona akerubi, anatambasula mapiko awo ndi kuwuluka. Pamene ankapita, mikombero inapita nawo pamodzi. Akerubi anakayima pa khomo la chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Tsono ulemerero wowala wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo.
Izi ndizo zamoyo ndinaziona pansi pa Mulungu wa Israeli ku mtsinje wa Kebara, ndipo ndinazindikira kuti anali akerubi. Kerubi aliyense anali ndi nkhope zinayi ndi mapiko anayi, ndipo kunsi kwa mapiko awo kunali chinthu chimene chimaoneka ngati manja a munthu. Nkhope zawo zinali zofanana ndi zomwe ndinaziona ku mtsinje wa Kebara. Kerubi aliyense amayenda molunjika.
Chiweruzo pa Atsogoleri a Israeli
Pamenepo Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kubwera nane ku chipata cha kummawa cha Nyumba ya Yehova. Kumeneko pa khomo la chipata panali anthu 25, ndipo ndinaona pakati pawo atsogoleri awa: Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi anthu amene akukonza zoyipa ndi kupereka malangizo oyipa mu mzindamo. Iwo amawuza anthu kuti, ‘Nthawi sinafike yoti timange Nyumba? Mzindawu uli ngati mʼphika umene uli pa moto ndipo ife tili ngati nyama mu mʼphikamo. Choncho iwe mwana wa munthu, unenere mowadzudzula. Nenera ndithu.’ ”
Ndipo Mzimu wa Yehova unandigwera ndipo unandiwuza kuti, “Unene kuti zimene akunena Yehova ndi izi. Iye akuti. ‘Izi ndi zimene mukunena, Inu Aisraeli, koma Ine ndikudziwa zimene zili mu mtima mwanu.’ Mwapha anthu ambiri mu mzinda muno ndipo mwadzaza misewu yake ndi mitembo.
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mitembo imene mwayiponya mʼmisewuyo ndiyo nyama ndipo mzinda uno ndiwo mʼphika, koma Ine ndidzakuthamangitsanimo. Inu mumaopa lupanga, koma lupangalo ndi limene ndidzakubweretsereni, akutero Ambuye. Ine ndidzakuthamangitsani mu mzinda ndipo ndidzakuperekani mʼdzanja la alendo kuti akulangeni. Mudzaphedwa ndi lupanga ndipo ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Mzinda uno sudzakhala ngati mʼphika wokutetezani ndipo simudzakhalanso ngati nyama ya mʼmenemo. Ndidzakulangani mpaka kumalire a Israeli. Ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Inu simunatsatire malangizo anga kapena kusunga malamulo anga koma mwakhala mukutsata zochita za mitundu ina ya anthu imene yakuzungulirani.’ ”
Tsono pamene ndinkanenera, Pelatiya mwana wa Benaya anafa. Pomwepo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba ndipo ndinafuwula ndi mawu aakulu kuti “Mayo, Ambuye Yehova! Kodi mudzawatheratu Aisraeli onse otsala?”
Yehova anayankhula nane kuti, “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”
Mulungu Alonjeza za Kubwerera kwa Israeli
“Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’
“Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.
“Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.
Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.
Chifaniziro cha Otengedwa Ukapolo
Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu owukira, iwowo maso openyera ali nawo, koma sakuona ndipo makutu omvera ali nawo, koma sakumva chifukwa choti ndi anthu owukira.
“Choncho, iwe mwana wa munthu, longedza katundu wako wopita naye ku ukapolo. Unyamuke nthawi yamasana iwo akuona. Uchite ngati wanyamuka kuchoka kumene ukukhala kupita ku dziko lachilendo iwowo akuona. Mwina adzamvetsetsa, paja ndi anthu aupandu. Utulutse katundu wako wopita naye ku ukapolo nthawi ya masana iwo akuona. Ndipo nthawi ya madzulo, iwo akuona, uchoke monga ngati ukupita ku ukapolo. Iwo akuona, ubowole pa khoma ndipo utulutsirepo katundu wako. Usenze katundu wako pa phewa iwo akuona, ndipo upite kunja ku mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi, pakuti ndakusandutsa iwe chizindikiro chochenjeza Aisraeli.”
Choncho ine ndinachita monga momwe anandilamulira. Nthawi yamasana ndinatulutsa zinthu zanga nditazimanga ngati ndikupita ku ukapolo. Ndipo nthawi yamadzulo ndinabowola khoma ndi manja anga. Pamene chisisira chinkayamba, ndinasenza katundu wanga pa phewa kutuluka naye iwo akuona.
Mmawa mwake Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu aupandu a Israeli sanakufunse kuti ukuchita chiyani?
“Uwawuze kuti, ‘zimene ndikunena Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndi izi: Uthengawu ndi wonena za kalonga wa ku Yerusalemu pamodzi ndi banja lonse la Israeli amene akukhala kumeneko.’ Uwawuze kuti, ‘Ndiwe chizindikiro chowachenjeza.’
“Zidzakuchitikirani monga momwe zakuchitikira iwemu. Iwo adzatengedwa kupita ku ukapolo.”
“Kalonga wawo adzatenga katundu wake nʼchisisira nʼkunyamuka. Adzatulukira pa bowo limene anthu anabowola pa khoma. Adzaphimba nkhope yake kuti asaone kumene akupita. Ndidzayala ukonde wanga pa iye ndi kumukola mu msampha wanga. Ndidzabwera naye ku Babuloni, dziko la Akaldeya, koma sadzaliona dzikolo, ndipo adzafera kumeneko. Ine ndidzabalalitsa kumbali zonse zinayi onse okhala naye pafupi, ndiwo omuthandiza ake pamodzi ndi ankhondo ake. Ndidzawalondola ndi lupanga losolola.
“Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwabalalitsira ku mayiko ena. Koma ndidzasiyako ena pangʼono amene adzapulumuke ku lupanga, njala ndi mliri, kuti akafotokoze ntchito zawo zonse zonyansa pakati pa anthu achilendo kumene akupitako. Pamenepo adzadziwa kuti ndine Yehova.”
Pambuyo pake Yehova anandiyankhulanso nati, “Iwe mwana wa munthu, uzinjenjemera ukamadya chakudya chako, ndipo uzinthunthumira ndi mantha ukamamwa madzi ako. Uwawuze anthu a mʼdzikomo kuti izi ndi zimene Ambuye Wamphamvuzonse akunena za anthu okhala mu Yerusalemu ndi dziko la Israeli: Iwo adzadya chakudya chawo ndi mantha ndi kumwa madzi awo ndi nkhawa. Zonse za mʼdziko lawo zidzalandidwa chifukwa cha ziwawa za anthu onse okhala mʼmenemo. Mizinda imene ili ndi anthu idzasakazika ndipo dziko lidzasanduka chipululu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Yehova anayankhulanso nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene ukunenedwa mu Israeli ndi wotani: ‘Masiku akupita koma masomphenya onse sakukwaniritsidwa?’ Choncho uwawuze anthuwo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndidzawuthetsa mwambi umenewu ndipo sadzawunenanso mu Israeli.’ Uwawuze kuti, ‘masiku ayandikira oti zonse zimene ndinanena mʼmasomphenya zichitikedi. Pakuti masiku amenewo sikudzakhalanso masomphenya abodza kapena kuwombeza kwa chinyengo pakati pa anthu a Israeli. Koma Ine Ambuye ndidzayankhula chimene ndikufuna, ndipo chidzachitikadi, osachedwa ayi. Pakuti mʼmasiku anu omwe ano, inu anthu opanduka, ndidzakwaniritsa chilichonse chimene ndidzanena. Ndikutero Ine Yehova.’ ”
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli akunena kuti, ‘masomphenya amene ukuona sadzachitika kwa zaka zambiri. Iwo akuti ukulosa za zinthu zimene zidzachitika ku tsogolo kwambiri.’
“Choncho uwawuze kuti, ‘zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena ndi izi: Zonena zanga sizidzachedwanso; chilichonse chimene ndikunena chidzachitikadi. Ndikutero Ine Yehova.’ ”
Mawu Odzudzula Aneneri Onyenga
Yehova anayankhulanso nane kuti, “Iwe mwana wa munthu unenere modzudzula aneneri a Israeli amene akunenera za kukhosi kwawo. Uwawuze iwowa kuti, ‘Imvani mawu a Yehova!’ Ambuye Yehova akuti, ‘Tsoka kwa aneneri opusa amene amangonenera zopeka ngakhale kuti sanaone kanthu konse!’ Iwe Israeli, aneneri ako ali ngati nkhandwe pa mabwinja. Simunakwere khoma kuti mukakonze mʼmene munagumuka, kuti Aisraeli adziteteze kolimba pa nkhondo pa tsiku la Yehova. Masomphenya awo ndi achabe ndipo kuwombeza kwawo ndi kwabodza. Iwo amati, ‘Yehova akutero,’ pomwe Yehova sanawatume. Komabe iwo amayembekezera kuti zimene ayankhulazo zichitikadi. Koma Ine ndikuti masomphenya anu ngachabechabe ndi zimene mwawombedzazo nʼzabodza. Mumanena kuti, ‘Akutero Yehova,’ pamene sindinayankhule nʼkomwe.
“Tsono Ine Ambuye Wamphamvuzonse ndikukutsutsani chifukwa cha zoyankhula zanu zonama ndi masomphenya anu abodzawo. Ndikutero Ine Yehova. Ndidzalanga aneneri amene amanenera zabodza za zinthu zimene amati anaziona mʼmasomphenya. Sadzakhala nawo mʼbwalo la anthu anga ndipo mayina awo sadzalembedwa mu kawundula wa nzika za Israeli. Sadzalowa nawo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
“Popeza kuti aneneri asocheretsa anthu anga pomanena kuti, ‘Kuli mtendere’ pamene mtendere palibe; ndiponso anthu akamanga khoma iwo nʼkumalipaka njereza, choncho ufotokozere amene alipaka njerezawo kuti khomalo lidzagwa. Mvula idzagwa mwamphamvu, kudzagwa matalala akuluakulu, ndipo kudzawomba mphepo yamkuntho. Pamene khomalo lagwa, kodi anthu sadzakufunsani kuti, ‘Kodi njereza yemwe munapaka uja ali kuti?’
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti: Mwa ukali ndidzakunthitsa mphepo ya mkuntho. Ndidzagwetsa matalala akuluakulu ndili ndi ukali ndipo ndidzavumbwitsa mvula yamphamvu ndi mkwiyo mpaka khomalo litawonongeka kotheratu. Ndidzagwetsa khoma limene munalipaka njerezalo. Ndidzaligumuliratu mpaka pansi kotero kuti maziko ake adzaoneka. Khomalo likadzagwa, inu mudzawonongekamo; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Kotero ndidzagwiritsa ntchito mkwiyo wanga pa khomali ndi pa amene analipaka njereza. Pambuyo pake ndidzakuwuzani kuti, ‘Khoma lagwa pamodzi ndi amene analipaka njereza. Agwanso aneneri a Yerusalemu amene ankalosa za Yerusalemu nʼkumati anaona mʼmasomphenya za mtendere wa Yerusalemu pamene mtendere kunalibe konse, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.’
“Tsono iwe mwana wa munthu, yankhulapo pa nkhani za akazi amene ali pakati pa anthu ako. Iwo amanenera zopeka za mʼmutu mwawo. Tsono adzudzule. Uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Tsoka kwa akazi amene amasoka zithumwa zapamkono, amenenso amasoka nsalu za kumutu za anthu. Kodi mufuna kukola mitima ya anthu anga, inuyo nʼkupulumutsa moyo wanu? Ponamiza anthu anga amene amamva za mabodza anu, inu mwapha anthu amene sanayenera kufa ndipo mwasiya ndi moyo amene sanayenera kukhala ndi moyo.
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikudana ndi zithumwa zanu zimene mumakokera nazo mitima ya anthu ngati mbalame. Ndidzazingʼamba kudzichotsa pa mikono yanu. Choncho ndidzapulumutsa miyoyo ya anthu amene munawakola ngati mbalame. Ndidzangʼamba nsalu zanu za matsengazo ndi kupulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu, ndipo simudzakhalanso ndi mphamvu yowakolera. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Popeza kuti munatayitsa mtima anthu olungama ngakhale sindinafune kuti ataye mtima; ndipo munalimbitsa anthu oyipa kuti asaleka machimo awo motero sakutha kupulumutsa moyo wawo, choncho inu simudzaonanso masomphenya abodza kapena kuwombeza. Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu. Ndipo pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Yehova Adzudzula Opembedza Mafano
Tsiku lina ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kwa ine ndipo anakhala pansi pamaso panga. Ndipo Yehova anandipatsa uthenga uwu nati, “Iwe mwana wa munthu, anthu awa ayika mtima pa mafano awo. Ayikanso maso awo pa zinthu zina zoyipa zopunthwitsa. Kodi ayembekezera kuti ndiwayankhe chimene atandifunse? Tsono yankhula nawo ndi kuwawuza kuti zimene akunena Ambuye Yehova: ‘Ngati Mwisraeli aliyense ayika mtima wake pa mafano ndi kuyika maso ake pa zinthu zoyipa zopunthwitsa, kenaka nʼkupita kwa mneneri, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha molingana ndi kuchuluka kwa mafano ake. Ine ndidzachita zimenezi kuti mwina nʼkukopa mitima ya anthu a Israeli, amene andisiya chifukwa cha mafano awo.’
“Nʼchifukwa chake uwawuze Aisraeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Lapani! Siyani mafano anu ndi ntchito zanu zonse zonyansa!
“ ‘Ngati Mwisraeli wina aliyense kapena mlendo wina aliyense wokhala pakati pa Israeli adzichotsa yekha kwa Ine ndi kuyika mtima pa mafano ake ndi kuyikanso maso ake pa zinthu zopunthwitsa ndipo kenaka nʼkupita kwa mneneri kukafunsa nzeru, Ineyo Yehova mwini wakene ndidzamuyankha. Ine ndidzalimbana naye munthu ameneyo ndipo ndidzamusandutsa chitsanzo ndi chisudzo. Ndidzamuchotsa pakati pa anthu anga. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Ndipo ngati mneneri anyengedwa nanenera, Ine Yehova ndiye ndamunyenga mneneri ameneyo, ndipo ndidzatambasula dzanja langa kumukantha ndi kumuwononga pakati pa anthu anga Aisraeli. Iwo adzalangidwa chifukwa cha kulakwa kwawo. Chilango cha wodzafunsira nzeru kwa mneneri chidzafanana ndi chilango cha mneneriyo. Ndidzachita zimenezi kuti Aisraeli asasocherenso kundisiya Ine ndi kuti asadziyipitsenso ndi machimo awo. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Chilango Chosathawika
Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko lindichimwira posandikhulupirira, Ine ndidzatambasula dzanja langa kulikantha pochepetsa chakudya chake. Ndidzatumiza njala pa dzikolo ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. Ngakhale anthu atatu awa, Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, akanangopulumutsa moyo wawo chifukwa cha chilungamo chawo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“Kapena ndikanatumiza zirombo mʼdziko monse ndi kulisiya lopanda anthu, ndipo dzikolo nʼkukhala chipululu chakuti munthu sangadutse chifukwa cha zirombo. Apanso, ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo okha akanapulumuka, koma dziko likanasanduka chipululu.’
“Kapena ndikanatumiza lupanga mʼdzikolo ndi kunena kuti, ‘Lupanga lipite mʼdziko monse,’ ndi kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Ngakhale anthu atatu awa akanakhalamo, sakanatha kupulumutsa ana awo aamuna kapena ana aakazi. Iwo okha akanapulumuka.’
“Kapena ndikanatumiza mliri mʼdzikomo ndi kuonetsa ukali wanga pokhetsa magazi, kuwononga anthu ake ndi nyama zomwe. Apanso ndikunenetsa Ine Ambuye Yehova kuti ngakhale Nowa, Danieli ndi Yobu akanakhala mʼmenemo, sakanatha ngakhale kupulumutsa mwana wamwamuna kapena wamkazi. Akanangodzipulumutsa okha chifukwa cha chilungamo chawo.
“Pakuti Ambuye Yehova akuti: Kudzakhala zoopsa kwambiri pamene ndidzatumiza pa Yerusalemu zilango zanga zinayi izi: lupanga, njala, zirombo ndi mliri kuti ziwononge anthu ake ndi nyama zomwe! Komabe padzakhala ena opulumuka, ana aamuna ndi ana aakazi amene adzatulutsidwa mʼdzikomo. Iwo adzabwera kwa inu, ndipo mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo, mitima yanu idzakhala pansi mukadzakumbukira chilango chimene ndinachita pa Yerusalemu. Mitima yanu idzakhala pansi mukadzaona makhalidwe awo ndi zochita zawo. Tsono mudzadziwa kuti Yerusalemu sindinamuchite zimenezi popanda chifukwa, akutero Ambuye Yehova.”
Yerusalemu, Mtengo Wamphesa Wosabereka
Yehova anayankhulanso nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wamphesa umapambana bwanji mtengo wina uliwonse? Nthambi zake zimapambana bwanji nthambi ina iliyonse. Mtengo umene uja nʼkupangira chiyani? Kodi anthu angathe kupangira chikhomo chokolekapo zinthu zawo? Taonani, ndi nkhuni chabe zosonkhera moto. Ukaponyedwa pa moto monga nkhuni ndi kuyaka mbali zonse ndi kusanduka makala, kodi ungagwiritsidwe ntchito ina iliyonse? Ngati pamene unali wosapsa sukanatheka kuwugwiritsa ntchito, nanga bwanji utapserera ndi moto, adzawugwiritsa ntchito bwanji?
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Mtengo wamphesa ndidzawuponya mʼmoto monga ndimachitira ndi mitengo ina ya ku nkhalango. Momwemonso ndidzachita ndi anthu a ku Yerusalemu. Ndidzawalanga pamenepo ngakhale iwo atuluka pa moto, motowo udzawatenthabe. Ndipo pamene ndidzatsutsana nawo, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ine ndidzasandutsa dziko kukhala chipululu chifukwa anthu akhala osakhulupirika, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Kusakhulupirika kwa Yerusalemu
Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, udzudzule Yerusalemu za ntchito zake zonyansa. Umuwuze kuti, ‘Ambuye Yehova akukuwuza, iwe Yerusalemu kuti: Kwawo kwa makolo ako ndi ku Kanaani ndipo iwe unabadwira komweko. Abambo ako anali Mwamori, amayi ako anali Mhiti. Pa tsiku lomwe unabadwa sanadule mchombo wako. Sanakusambitse mʼmadzi kuti uyere. Sanakuthire mchere kapena kukukulunga mʼnsalu. Palibe ndi mmodzi yemwe anakusamala kapena kukumvera chisoni kuti akuchitire zimenezi. Mʼmalo mwake anakutaya panja poyera, chifukwa ananyansidwa nawe pa tsiku lako lobadwa.
“ ‘Tsono pamene ndinkadutsa, ndinakuona ukuvimvinizika mʼmagazi ako. Ndinakuyankhula uli mʼmagazi ako omwewo kuti, ‘Khala ndi moyo,’ ndi kuti ukule ngati mbewu ya mʼmunda. Iwe unakula ndipo unatalika ndi kutha msinkhu. Mawere ako anayamba kumera ndi tsitsi lakonso linayamba kutalika. Komabe unali wamaliseche ndi wausiwa.
“ ‘Tsono pamene ndinkadutsanso ndinaona kuti nthawi yako yomanga banja inakwana. Tsono ndinakufunditsa chovala changa ndi kubisa umaliseche wako. Ndinachita nawe pangano la ukwati ndipo unakhala wanga, akutero Ambuye Wamphamvuzonse.
“ ‘Ine ndinakusambitsa mʼmadzi kutsuka magazi ako ndikukudzoza mafuta. Ndinakuveka zovala zopetapeta ndi nsapato za chikopa. Ndinakuveka zovala zabafuta ndi kukuveka zovala za bafuta. Ndinakukongoletsa ndi zokometsera zamtengowapatali: ndinakuveka zibangiri mʼmanja mwako ndi mkanda mʼkhosi mwako, ndipo ndinakuveka chipini pa mphuno yako, ndolo ku makutu ako ndiponso chipewa chaufumu pa mutu wako. Choncho unavala zokongoletsa zagolide ndi siliva. Zovala zako zinali zabafuta, zasilika ndi za nsalu zopetapeta. Chakudya chako chinali ufa wosalala uchi ndi mafuta a olivi. Motero unakhala wokongola kwambiri ndipo unasanduka mfumukazi. Ndipo mbiri ya kukongola kwako inawanda pakati pa anthu a mitundu ina, chifukwa ulemerero umene ndinakupatsa unapititsa patsogolo kukongola kwako, akutero Ambuye Yehova.
“ ‘Koma iwe unatama kukongola kwako ndipo unayamba kuchita zadama chifukwa cha kutchuka kwako. Unkachita chigololo ndi kumangodzipereka kwa aliyense wodutsa ndipo kukongola kwako kunakhala kwake. Unatenga zovala zako zina nukakongoletsera malo opembedzerako mafano, ndipo kumeneko umachitirako zigololo. Zinthu izi sizinachitikepo nʼkale lomwe ndipo sizidzachitikanso. Unatenga zokongoletsera zopangidwa ndi golide ndi siliva zimene ndinakupatsa ndipo unadzipangira wekha mafano aamuna amene unkachita nawo za dama. Ndipo iwe unatenga zovala zako zopetapeta ndi kuveka mafano. Mafuta anga ndi lubani wanga unapereka kwa mafanowo. Chakudya chimene ndinakupatsa, ufa, mafuta ndi uchi, zimene ndinkakudyetsa nazo unazitenga nʼkuzipereka kwa mafanowo ngati nsembe ya fungo lokoma. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo? Chifukwa cha zadama zako zonyansazi unayiwala masiku a ubwana wako pamene unali wamaliseche, wausiwa ndiponso womangovivinizika mʼmagazi.
“ ‘Tsoka! Tsoka kwa iwe, akutero Ambuye Yehova chifukwa powonjezera pa zoyipa zako zonse, wadzimangira wekha nsanja ndi guwa pa mabwalo onse. Pa msewu uliwonse wamanga nsanjazo. Motero wanyazitsa kukongola kwako podzipereka kwa aliyense amene adutsapo. Umachita chigololo ndi Aigupto, anthu adama oyandikana nawe. Choncho unandikwiyitsa chifukwa unachulukitsa za dama zako. Nʼchifukwa chake ndinatambasula dzanja langa kukukantha ndi kuchepetsa dziko lako. Ndinakupereka kwa adani ako, Afilisti amene amayipidwa ndi makhalidwe ako onyansa. Chifukwa cha chilakolako chako unachitanso zadama ndi Aasiriya. Ngakhale unachita nawo chigololo koma sunakhutitsidwebe. Choncho unapitirirabe kuchita chigololo ndi Ababuloni, anthu a mʼdziko lokonda zamalonda. Ngakhale unachita izi, komabe sunakhutitsidwe.
“ ‘Ambuye Yehova akuti: Mtima wako ndi wofowoka kwambiri chifukwa unachita zonsezo monga ngati mkazi wopanga manyazi. Unamanga nsanja pa msewu uliwonse. Unamanganso kachisi pabwalo lililonse. Komabe sunachite ngati mkazi wadama chifukwa unakana malipiro.
“ ‘Iwe mkazi wachigololo! Umakonda amuna achilendo kupambana mwamuna wakowako! Amuna ndiwo amapereka malipiro kwa mkazi wadama. Koma iwe ndi amene ukupereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse. Choncho umazinyengerera kuti zizibwera kwa iwe kuchokera mbali zonse kudzagona nawe. Chotero iwe ukusiyana ndi akazi ena achigololo, pakuti palibe amene ankakunyengerera kuti uchite naye chigololo. Iweyo ndiye unkapereka ndalama osati ena kukupatsa ndalama ayi. Motero unalidi wosiyana kwambiri ndi akazi ena.
“ ‘Tsono mkazi wachigololo iwe, imva mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti, popeza unavula ndi kuonetsa umaliseche wako mopanda manyazi, unachita chigololo ndi zibwenzi zako pamodzi ndi mafano ako onyansa, komanso popeza unapereka ana ako kuti aphedwe ngati nsembe zoperekedwa kwa mafano, nʼchifukwa chake Ine ndidzasonkhanitsa zibwenzi zako zonse, zimene unkasangalala nazo, amene unkawakonda ndi amene unkawada. Ndidzawasonkhanitsa motsutsana nawe kuchokera ku madera onse okuzungulira ndipo Ine ndidzakuvula pamaso pawo, ndipo iwo adzaona umaliseche wako wonse. Ine ndidzakulanga monga mmene amalangira akazi amene amachita chigololo ndiponso opha anthu. Chifukwa cha ukali wanga ndi nsanje yanga, ndidzakhetsa magazi ako mokwiya kwambiri. Ndidzakupereka mʼmanja mwa zibwenzi zako ndi kuwononga nyumba zopembedzera mafano ako. Iwo adzakuvula zovala zako ndi kutenga zodzikometsera zako zabwino. Choncho adzakusiya wa maliseche ndi wausiwa. Iwo adzabweretsa gulu la anthu limene lidzakuponya miyala ndi kukutematema ndi malupanga awo. Adzatentha nyumba zako ndi kukulanga iwe pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa chigololo chako, ndipo sudzalipiranso zibwenzi zako. Ukali wanga udzalekera pamenepo ndipo sindidzakuchitiranso nsanje. Ndidzakhala chete osakwiyanso.
“ ‘Popeza sunakumbukire masiku a ubwana wako koma unandikwiyitsa ndi zinthu zonsezi, Ine ndidzakubwezera ndithu chilango pamutu pako chifukwa cha zimene wachita, akutero Ambuye Yehova. Paja unawonjezera chigololo pa machitidwe ako onyansa.
“ ‘Taona, onse onena miyambi adzakuphera mwambi wakuti, ‘Make mbuu, mwana mbuu.’ Ndiwedi mwana weniweni wamkazi wa mayi wako, amene amanyoza mwamuna wake ndi ana ake. Ndiwe mʼbale weniweni wa abale ako, amene amanyoza amuna awo ndi ana awo. Amayi ako anali Mhiti ndipo abambo ako anali Mwamori. Mkulu wako anali Samariya, ndipo iye pamodzi ndi ana ake aakazi ankakhala cha kumpoto kwako. Mngʼono wako, Sodomu ankakhala cha kummwera kwako pamodzi ndi ana ake aakazi. Iwe sunangotsatira kokha njira zawo zoyipa ndi kuchita zonyansa zawo, koma patangopita nthawi pangʼono machitidwe ako oyipa anaposa awo. Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ngakhale mʼbale wako Sodomu ndi ana ake aakazi sanachitepo zimene iwe ndi ana ako aakazi munachita.
“ ‘Tsono tchimo la mʼbale wako Sodomu linali ili: Iye ndi ana ake aakazi ankanyadira kuchuluka kwa chakudya ndi chuma chawo. Koma sanalabadireko kuthandiza osauka ndi aumphawi. Anali odzitukumula ndipo ankachita zonyansa pamaso panga. Nʼchifukwa chake ndinawachotsa monga mmene waoneramu. Samariya sanachite ngakhale theka la machimo amene unachita. Iwe wachita zinthu zonyansa zambiri kuposa iwo, motero kuti abale ako awiriwo amaoneka ngati olungama kuyerekeza ndi iye. Tsono iwenso uyenera kuchita manyazi popeza waonetsa abale ako ngati osachimwa. Popeza kuti machimo ako ndi onyansa kwambiri kupambana awo, tsonotu iwowo akuoneka olungama kupambana iweyo. Choncho iwenso uchite manyazi ndi kunyozedwa popeza unaonetsa abale ako ngati olungama.
“ ‘Koma, ndidzadalitsanso Sodomu ndi ana ake aakazi. Ndidzadalitsanso Samariya ndi ana ake aakazi. Pa nthawi yomweyo ndidzakudalitsanso iwe Yerusalemu. Ndidzatero kuti uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa cha zonse zimene unachita powatonthoza anthuwa. Motero mʼbale wako Sodomu ndi ana ake akadzakhala monga mmene analili poyamba paja, ndiponso mʼbale wako Samariya akadzakhalanso monga mmene anali poyamba paja, ndiye kuti iwenso ndi ana ako mudzakhala monga mmene munalili payamba paja. Kale lija pamene unkanyada, suja unkanyogodola mʼbale wako Sodomu kuyipa kwako kusanadziwike? Koma tsopano wafanana naye. Wasandukano chinthu chonyozeka kwa anthu a ku Edomu ndi kwa onse owazungulira ndiponso kwa Afilisti. Ndithu onse amene akuzungulira amakunyoza. Choncho udzalangidwa chifukwa cha zigololo zako ndi machitidwe anu onyansa, akutero Yehova.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulanga molingana ndi zimene unachita. Iwe unanyoza lumbiro lako pophwanya pangano langa. Komabe, Ine ndidzakumbukira pangano limene ndinachita nawe mʼmasiku a unyamata wako, ndipo ndidzakhazikitsa pangano losatha ndi iwe. Tsono udzakumbukira njira zako zakale. Udzachita manyazi polandiranso abale ako, wamkulu ndi wamngʼono yemwe. Ndidzawaperekanso kwa iwe kuti akhale ngati ana ako ngakhale kuti sali a mʼpangano langa ndi iwe. Kotero ndidzakhazikitsa pangano langa ndi iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndikadzakukhululukira zoyipa zako zonse zimene unachita, udzazikumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri, kotero kuti sudzatha nʼkuyankhula komwe, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Fanizo la Ziwombankhanga Ziwiri ndi Mtengo Wamphesa
Yehova anayankhula nane kuti, “Iwe mwana wa munthu, aphere mwambi anthu a Israeli ndi kuwawuza fanizo. Uwawuze kuti Ambuye Yehova akuti, chiwombankhanga chachikulu, cha mapiko amphamvu, nthenga zitalizitali zamathothomathotho chinabwera ku Lebanoni. Chinagwira nthambi ya pamwamba pa mtengo wa mkungudza. Chinabudula msonga yeniyeni ya nthambiyo nʼkupita nayo ku dziko lamalonda ndipo anakayika mu mzinda wa anthu amalonda.
“ ‘Kenaka chinatenga mbewu ina ya mʼdziko ndi kukayidzala ku malo a chonde kumene kunali madzi ambiri. Anayidzala ngati mmene amadzalira mtengo wa msondozi. Ndipo inaphuka nisanduka mtengo wa mpesa wotambalala chamʼmunsi. Nthambi zake zinaloza mmwamba kumene kunali chiwombankhangacho, koma mizu yake inalowa pansi. Kotero unakhala mtengo wamphesa ndipo unasanduka wa nthambi ndiponso wa masamba ambiri.
“ ‘Koma panali chiwombankhanga chinanso chachikulu, cha mapiko amphamvu ndi cha nthenga zambiri. Tsopano mtengo wamphesa uja unakhotetsera mizu yake kwa chiwombankhangacho kuchokera pa malo amene unadzalidwa ndipo unatambalitsa nthambi zake kwa chiwombankhangacho kufuna kuthiridwa madzi. Koma mtengowo unadzalidwa kale pa nthaka yabwino mʼmbali mwa madzi kuti ukhale ndi nthambi zambiri, ubereke zipatso ndi kukhala wokongola.’
“Ukawawuze Aisraeli kuti, ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Kodi udzakula bwino? Kodi chiwombankhanga chija sichidzawuzula mizu ndi kubudula nthambi zake kuti ufote? Masamba ake onse anthete adzafota. Sipadzafunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti awuzule. Ngakhale utawokedwa pena, kodi udzaphuka? Kodi sudzafoteratu mphepo ya kummawa ikadzawomba, kufotera pa malo pamene anawuwokerapo?’ ”
Kenaka Yehova anandiyankhula nati: “Tawafunsa anthu owukirawa kuti, ‘kodi mukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Uwafotokozere kuti, ‘Mfumu ya Babuloni inapita ku Yerusalemu ndikukatengako mfumu ndi anthu ake otchuka ndi kubwera nawo ku Babuloni. Ndipo anatenga mmodzi wa banja laufumu ndi kuchita naye mgwirizano, ndipo anamulumbiritsa kuti akhale womvera. Inatenganso akulu onse a mʼdzikomo kuti ufumu wa dzikolo utsitsidwe, usadzaphukenso, koma kuti ukhalepobe posunga pangano limene unachita. Koma mfumu inawukira mfumu ya ku Babuloni potumiza nthumwi ku dziko la Igupto kukatenga akavalo ndi gulu lalikulu la nkhondo. Kodi mfumu yotereyi ingapambane? Kodi wochita zinthu zoterezi angapulumuke? Kodi angaphwanye mgwirizano ndi kupulumuka?
“ ‘Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, mfumuyo idzafera ku Babuloni, mʼdziko la mfumu imene inayika pa mpando waufumu. Inapeputsa lumbiro lake nʼkuphwanya pangano limene inachita ndi mfumu inayo. Farao ndi gulu lake lankhondo lamphamvu sadzatha kumuthandiza pa nkhondo, pamene mfumu ya Babuloni idzapanga mitumbira ya nkhondo ndi nsanja za nkhondo kuti iwononge miyoyo yambiri. Mfumu ya ku Yuda inanyoza lumbiro lake pophwanya pangano. Inalonjeza komabe sinatsatire malonjezo ake. Choncho sidzapulumuka.
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndithu pali Ine wamoyo, Ine ndidzalanga mfumu imeneyi chifukwa inanyoza lumbiro langa, ndi kuphwanya pangano langa. Ndidzayitchera ukonde ndipo idzakodwa mu msampha wanga. Ndidzapita nayo ku Babuloni ndi kuyilanga kumeneko chifukwa inali yosakhulupirika kwa Ine. Asilikali ake onse amene akuthawa adzaphedwa ndi lupanga, ndipo opulumuka adzabalalitsidwa ku mbali zonse. Ndipo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova ndayankhula.
“ ‘Ambuye Yehova akuti: Ine mwini ndidzatenga nthambi pamwamba penipeni pa mkungudza ndi kuyidzala; ndidzathyola nthambi yanthete kuchokera pa nthambi zapamwamba penipeni ndi kuyidzala pamwamba pa phiri lalitali. Ndidzayidzaladi pa phiri lalitali la Israeli. Idzaphuka nthambi ndi kubereka zipatso. Choncho idzasanduka mkungudza wamphamvu. Mbalame za mtundu uliwonse zidzamanga zisa zawo mʼmenemo; zidzapeza malo okhala mu mthunzi wa nthambi zake. Mitengo yonse yakuthengo idzadziwa kuti Ine ndine Yehova amene ndimafupikitsa mitengo yayitali ndi kutalikitsa mitengo yayifupi. Ndimawumitsa mitengo yabiriwiri ndi kubiriwitsa mitengo yowuma.
“ ‘Ine Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichita.’ ”
Munthu Wochimwa Adzafa
Yehova anandiyankhula nati: “Kodi anthu inu mumatanthauza chiyani mukamabwerezabwereza kunena mwambi uwu wokhudza dziko la Israeli kuti:
“ ‘Nkhuyu zodya akulu zimapota
ndi ana omwe?’ ”
“Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, simudzanenanso mwambi umenewu mu Israeli. Pakuti moyo uliwonse ndi wanga. Moyo wa abambo ndi wanga, wamwananso ndi wanga. Munthu wochimwa ndi amene adzafe.
“Tiyerekeze kuti pali munthu wolungama
amene amachita zolungama ndi zolondola.
Iye sadyera nawo pa mapiri a chipembedzo
kapena kupembedza mafano a Aisraeli.
Iye sayipitsa mkazi wa mnzake
kapena kugonana ndi mkazi pamene akusamba.
Iye sapondereza munthu wina aliyense,
koma amabwezera wangongole nʼchigwiriro chake.
Iye salanda zinthu za osauka,
koma amapereka chakudya kwa anthu anjala,
ndipo amapereka zovala kwa anthu ausiwa.
Iye sakongoletsa ndalama mwa katapira,
kapena kulandira chiwongoladzanja chachikulu.
Amadziletsa kuchita zoyipa
ndipo sakondera poweruza milandu.
Iye amatsatira malangizo anga,
ndipo amasunga malamulo anga mokhulupirika.
Munthu ameneyo ndi wolungama;
iye adzakhala ndithu ndi moyo,
akutero Ambuye Yehova.
“Tiyerekeze kuti munthu wolungama chotere wabala mwana chimbalangondo amene amakhalira kupha anthu ndi kuchita zinthu zina zotere. Iye nʼkumachita zinthu zimene ngakhale abambo ake sanachitepo.
“Amadyera nawo ku mapiri achipembedzo.
Amayipitsa mkazi wa mnzake.
Iye amapondereza munthu wosauka ndi wosowa.
Amalanda zinthu za osauka.
Sabweza chikole cha munthu wa ngongole.
Iye amatembenukira ku mafano
nachita zonyansa.
Iye amakongoletsa mwa katapira ndipo amalandira chiwongoladzanja chachikulu.
Kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu! Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, adzaphedwa ndipo adzalandira chilango chomuyenera.
“Tsono tiyerekeze kuti munthu woyipa uyu wabala mwana amene amaona machimo onse amene abambo ake ankachita. Ngakhale amaona koma osatsanzira ntchito zake zoyipazo.
“Sadyera nawo pa mapiri achipembedzo.
Sapembedza mafano a ku Israeli.
Sayipitsa mkazi wa mnzake.
Sapondereza munthu wina aliyense.
Satenga chikole akabwereketsa chinthu. Salanda zinthu za osauka.
Salanda zinthu za munthu.
Amapereka chakudya kwa anthu anjala.
Amapereka zovala kwa anthu aumphawi.
Amadziletsa kuchita zoyipa.
Sakongoletsa kuti apezepo phindu. Salandira chiwongoladzanja.
Amasunga malangizo anga ndi kumvera malamulo anga.
Munthu wotereyo sadzafa chifukwa cha machimo a abambo ake. Adzakhala ndi moyo ndithu. Koma abambo ake, popeza kuti anazunza anthu ena ndi kubera mʼbale wawo ndiponso popeza kuti sanachitire zabwino anansi ake, adzafera machimo ake omwe.
“Mwina inu mukhoza kufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwana salangidwa chifukwa cha kulakwa kwa abambo ake? Ayi, mwanayo adzakhala ndi moyo chifukwa ankachita zolungama ndi zolondola ndipo ankasamala kumvera malamulo anga onse. Munthu wochimwa ndiye amene adzafe. Mwana sadzapezeka wolakwa chifukwa cha abambo ake, kapena abambo kupezeka wolakwa chifukwa cha mwana wawo. Chilungamo cha munthu wolungama ndicho chidzamupulutse, ndipo kuyipa kwa munthu wochimwa ndiko kudzamuwonongetse.
“ ‘Munthu woyipa akatembenuka mtima ndi kusiya machimo amene ankachita ndi kuyamba kumvera malamulo anga ndi kumachita zolungama ndi zokhulupirika, ndiye kuti adzakhala ndi moyo. Sadzafa ayi. Zoyipa zake zonse zidzakhululukidwa. Chifukwa cha zinthu zolungama zimene anazichita adzakhala ndi moyo. Kodi Ine ndimakondwera ndi imfa ya munthu woyipa? Ayi, ndimakondwera pamene woyipa watembenuka mtima kuti akhale ndi moyo. Akutero Ambuye Yehova.
“ ‘Koma ngati munthu wolungama apatuka kusiya zachilungamo ndi kuyamba kuchita tchimo ndi zonyansa za mtundu uliwonse zimene amachita anthu oyipa, kodi munthu wotereyu nʼkukhala ndi moyo? Ayi ndithu, zolungama zake zonse sizidzakumbukiridwa. Iye adzayenera kufa chifukwa cha machimo amene anachita.
“Komabe inu mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Tamvani tsono inu Aisraeli: Kodi zochita zanga ndizo zosalungama? Kodi si zochita zanu zimene ndi zosalungama? Ngati munthu wolungama atembenuka kusiya chilungamo chake ndi kuchita tchimo, iye adzafa chifukwa cha tchimolo. Koma ngati munthu woyipa aleka zoyipa zake zimene anazichita ndi kuyamba kuchita zimene ndi zolungama ndi zolondola, iye adzapulumutsa moyo wake. Popeza waganizira za zolakwa zonse ankachita ndipo wazileka, iye adzakhala ndi moyo ndithu; sadzafa. Komabe Aisraeli akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Kodi zochita zanga ndizo zopanda chilungamo, inu Aisraeli? Kodi si zochita zanu zimene ndi zopanda chilungamo?
“Chifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: inu Aisraeli, Ine ndidzakuweruzani aliyense wa inu molingana ndi ntchito zake. Lapani! Lekani zoyipa zanu kuti musawonongeke nazo. Tayani zolakwa zanu zonse zimene munandichimwira nazo ndipo khalani ndi mtima watsopano ndi mzimu watsopano. Kodi muferanji inu Aisraeli? Ine sindikondwera ndi imfa ya munthu aliyense, akutero Ambuye Yehova. Chifukwa chake, lapani kuti mukhale ndi moyo.”
Nyimbo ya Maliro a Akalonga a Israeli
“Imba nyimbo ya madandawulo, kuyimbira akalonga a ku Israeli. Uzinena kuti,
“ ‘Amayi ako anali ndani?
Anali ngati mkango waukazi!
Iwo unabwatama pakati pa mikango yayimuna;
unkalera ana ake pakati pa misona.
Unalera mmodzi mwa ana ake,
ndipo mwanayo anasanduka mkango wamphamvu.
Unaphunzira kugwira nyama,
ndipo unayamba kudya anthu.
Anthu amitundu anamva za mkangowo,
ndipo tsiku lina unagwa mʼmbuna mwawo.
Iwo anawukoka ndi ngowe
kupita nawo ku dziko la Igupto.
“ ‘Amayi aja ataona kuti mwana ankamukhulupirira uja wagwidwa ndi kuti chiyembekezo chake chapita padera,
amayiwo anatenganso mwana wina
namusandutsa mkango wamphamvu.
Unkayendayenda pakati pa mikango inzake,
pakuti tsopano unali mkango wamphamvu.
Unaphunzira kugwira nyama
ndipo unayamba kudya anthu.
Unagwetsa malinga awo,
ndikuwononga mizinda yawo.
Onse a mʼdzikomo
anachita mantha chifukwa cha kubangula kwake.
Pamenepo mitundu ya anthu, makamaka ochokera madera ozungulira,
inabwera kudzalimbana nawo.
Anawutchera ukonde wawo,
ndipo tsiku lina unagwera mʼmbuna mwawo.
Anawukoka ndi ngowe nawuponya mʼchitatanga.
Anabwera nawo kwa mfumu ya ku Babuloni
ndipo mfumuyo inawuponya mʼndende
ndi cholinga choti liwu lake lisamamvekenso
ku mapiri a Israeli.
“ ‘Amayi ako anali ngati mpesa mʼmunda wamphesa
wodzalidwa mʼmbali mwa madzi.
Unabereka bwino ndipo unali ndi nthambi zambiri
chifukwa cha kuchuluka kwa madzi.
Nthambi zake zinali zolimba,
zoyenera kupangira ndodo yaufumu.
Unatalika nusomphoka pakati pa
zomera zina.
Unkaoneka bwino chifukwa cha kutalika kwake,
ndi nthambi zake zambiri.
Koma unazulidwa mwaukali
ndipo unagwetsedwa pansi.
Unawuma ndi mphepo ya kummawa,
zipatso zake zinayoyoka;
nthambi zake zolimba zinafota
ndipo moto unapsereza mtengo wonse.
Ndipo tsopano anawuwokeranso ku chipululu,
dziko lowuma ndi lopanda madzi.
Moto unatulukanso mu mtengomo
ndi kupsereza nthambi ndi zipatso zake.
Palibe nthambi yolimba inatsala pa mtengowo
yoyenera kupangira ndodo yaufumu.
Imeneyi ndi nyimbo yachisoni ndipo yasanduka nyimbo ya pa maliro.’ ”
Kuwukira kwa Israeli
Tsiku lakhumi la mwezi wachisanu, chaka chachisanu ndi chiwiri, ena mwa akuluakulu a Israeli anabwera kudzapempha nzeru kwa Yehova, ndipo anakhala pansi pamaso panga.
Tsono Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, ayankhule akuluakulu a Israeli ndi kuwawuza kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Kodi mwabwera kudzapempha nzeru kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, Ine sindidzakulolani kupempha nzeru kwa Ine, akutero Ambuye Yehova.’
“Kodi uwaweruza? Iwe mwana wa munthu, kodi ugamula mlandu wawo? Uwadziwitse tsono zonyansa zimene anachita makolo awo, uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Pa tsiku limene ndinasankha Israeli, ndinalumbira kwa zidzukulu za nyumba ya Yakobo ndipo ndinadziwulula kwa iwo ku Igupto. Ndinalumbira ndi kuwawuza kuti: Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Pa tsiku limenelo ndinalumbira kwa iwo kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kupita nawo ku dziko limene ndinawapezera, dziko la mwana alirenji, dziko lokongola kwambiri kupambana mayiko ena. Ndipo ndinawawuza kuti, ‘Aliyense ataye zinthu zonse zonyansa zimene ankasangalala nazo, ndipo musadziyipitse ndi mafano a Igupto, Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
“ ‘Koma iwo anandiwukira ndipo sanafune kundimvera. Palibe amene anataya zonyansa zonse zimene ankasangalala nazo. Panalibenso amene anasiya mafano a ku Igupto. Tsono ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwaonetsa mkwiyo wanga mʼdziko la Igupto momwemo. Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene ankakhala pakati pawo. Paja ndinali nditaonetsa mphamvu zanga pamaso pa mitunduyo potulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto. Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi kubwera nawo mʼchipululu. Ndinawapatsa malangizo anga ndi kuwadziwitsa malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndinawapatsanso Masabata ngati chizindikiro pakati pathu, kuti adziwe kuti Ine Yehova ndinawapatula.
“ ‘Komabe anthu a Israeli anandiwukira mʼchipululu. Iwo sanatsatire malangizo anga koma anakana malamulo anga amene munthu aliyense akawamvera adzakhala ndi moyo. Ndipo anayipitsa kotheratu Masabata anga. Choncho, ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawononga mʼchipululu. Koma sindinachite zimenezi chifukwa cha dzina langa, kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Igupto. Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu muja, nditakweza dzanja, kuti sindidzawalowetsanso mʼdziko limene ndinawapatsa, dziko la mwana alirenji, lokoma kwambiri kuposa mayiko ena onse. Paja anakana malamulo anga, sanatsatire malangizo anga ndipo anayipitsa masabata anga. Mitima yawo inakonda mafano. Komabe ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge kapena kuwatheratu mʼchipululu. Tsono kwa ana awo mʼchipululu ndinati, ‘Musatsatire malangizo a makolo anu kapena kusunga malamulo awo kapena kudziyipitsa ndi mafano awo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu; tsatirani malangizo anga ndipo sungani malamulo anga. Masabata anga muziwasunga ngati opatulika kuti akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi inu. Mukatero mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’
“ ‘Koma ana awo anandiwukira. Iwo sanatsatire malangizo anga, sanamvere malamulo anga, ngakhale kuti amapereka moyo kwa munthu amene amawamvera. Ndiponso anayipitsa Masabata anga. Choncho ndinaganiza zowakhuthulira ukali wanga ndi kuwawonongeratu mʼchipululu momwemo. Koma sindinatero chifukwa cha dzina langa kuti lisayipitsidwe pakati pa anthu a mitundu ina amene anandiona ndikutulutsa Aisraeliwo mu Iguptomo. Choncho ndinalumbira mʼchipululu, nditakweza dzanja langa, kuti ndidzawabalalitsa pakati pa anthu a mitundu ina ndi kuwamwazira ku mayiko akutali, chifukwa sanamvere malamulo anga, anakana malangizo anga, nayipitsa masabata anga, ndi kupembedza mafano a makolo awo. Ine ndinawapatsanso malangizo amene sanali abwino ndi malamulo amene sakanatha kupeza nawo moyo. Ndinawalekerera kuti adziyipitse ndi mphatso zawo zomwe, makamaka popereka ana awo oyamba kubadwa ngati nsembe zopsereza. Ndinatero kuti ndiwadetse nkhawa ndi kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova.’
“Tsono iwe mwana wa munthu, yankhula nawo Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ambuye Yehova akuti makolo anu anandinyozanso posaonetsa moyo wokhulupirika. Nditawalowetsa mʼdziko limene ndinachita kulumbirira kuti ndidzawapatsa, iwo tsono ankapita kulikonse kumene anaona chitunda chachitali ndi mtengo wa masamba ambiri kukapereka kumeneko nsembe ndi zopereka zawo zimene zinkandikwiyitsa. Kumeneko ankapereka nsembe za fungo lokoma ndiponso nsembe za zakumwa. Tsono ndinawafunsa kuti: Kodi chitunda chimene mukupitako nʼchotani? Chitundachi chakhala chikutchedwa mpaka lero kuti ‘Chitunda cha Chipembedzo.’
Chiweruzo ndi Kubwezeretsa
“Tsono uwawuze Aisraeli kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi mudzadziyipitsa nokha monga anachitira makolo anu ndi kuchita chigololo ndi milungu yawo yonyansa? Pamene mubwera kudzapereka mphatso zanu ndi kudzapereka ana kuti akhale ngati nsembe zopsereza mumadziyipitsa ndi mafano anu mpaka lero. Kodi Aisraeli, ndingathe kukulolani bwanji kuti mulandire malangizo kwa Ine? Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, sindidzalola kuti mupemphe nzeru kwa Ine.
“ ‘Inu munanena kuti, ‘Tikufuna tikhale ngati anthu a mitundu ina, ngati anthu adziko lapansi, amene amapembedza mtengo ndi mwala.’ Koma zimene mukuganizazo sizidzachitika. Ndithu pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Yehova, ndi dzanja langa lamphamvu, nditasamula mkono wanga mokwiya kwambiri, Ine ndidzakhala wokulamulani. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndikukusonkhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munamwazikirako, ndi dzanja langa lamphamvu ndi lotambasuka ndili wokwiya kwambiri. Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha anthu a mitundu ina ndipo kumeneko, moonana maso ndi maso, ndidzakuzengani mlandu. Monga ndinawalangira makolo anu mʼchipululu cha dziko la Igupto, motero ndidzakulangani, akutero Ambuye Yehova. Ndidzakuwerengani ndi ndodo ya mʼbusa, kukulowetsani mʼchimango cha pangano langa. Ndidzakuchotserani anthu amene anandigalukira ndi kundiwukira. Ngakhale ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo, koma sadzalowamo mʼdziko la Israeli. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Koma inu Aisraeli, zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Pitani katumikireni mafano anu onse, aliyense wa inu! Koma mʼtsogolo mwake mudzandimvera ndithu ndipo simudzayipitsa dzina langa lopatulika popereka mphatso zanu kwa mafano. Pakuti pa phiri langa lopatulika, phiri lalitali la ku Israeli, akutero Ambuye Yehova, Aisraeli onse adzanditumikira, ndipo kumeneko Ine ndidzawalandira. Kumeneko ndidzayembekeza zopereka zanu ndi mphatso zanu zopambana, pamodzi ndi nsembe zanu zonse zopatulika. Ndidzakulandirani ngati nsembe ya fungo lokoma ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusokhanitsani kuchokera ku mayiko kumene munabalalitsidwirako. Motero ndidzadzionetsa pakati panu kuti ndine woyera ndipo mitundu ya anthu idzaona. Tsono mudzadziwa kuti ndine Yehova ndikadzabwera nanu ku dziko la Israeli, dziko limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa makolo anu. Kumeneko mudzakumbukira makhalidwe anu ndi machitidwe anu onse amene munadziyipitsa nawo, ndipo mudzanyansidwa nokha chifukwa cha zoyipa zimene munachita. Inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzakuchitirani zabwino chifukwa cha dzina langa koma osati molingana ndi njira zanu zoyipa ndi machitidwe anu okhota, inu Aisraeli, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Uneneri Wotsutsa Kummwera
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane kummwera; ndipo lalika mawu odzudzula anthu akummwera ndipo unenere zodzudzula dziko la nkhalango ya kummwera. Iwuze nkhalango yakummwera kuti, ‘Imvani mawu a Yehova! Ambuye Yehova akuti: Ndikuyatsa moto ndipo motowo udzapsereza mitengo yako yonse yayiwisi ndi yowuma yomwe. Malawi ake sadzazimitsika ndipo aliyense kuchokera kummwera mpaka kumpoto adzapsa nawo. Aliyense adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndayatsa motowo, ndipo sudzazimitsidwa.’ ”
Ndipo ine ndinati, “Aa, Ambuye Yehova! Anthu akungondinena kuti, ‘Kodi suja amangonena nthano chabe ameneyu!’ ”
Babuloni, Lupanga la Mulungu
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, tembenuka uyangʼane ku Yerusalemu ndipo ulalike mawu odzudzula malo ake opatulika. Unenere zodzudzula anthu a ku Yerusalemu. Uwawuze kuti, Ambuye Yehova akuti, ‘Taona, Ine ndidzalimbana nawe. Ndidzasolola lupanga langa mʼchimake ndi kuwononga anthu olungama ndi ochimwa omwe. Motero ndidzapha aliyense kuchokera kummawa mpaka kumpoto. Pamenepo anthu onse adzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndasolola lupanga langa mʼchimake; sindidzalilowetsanso mʼchimakemo.’
“Tsono iwe mwana wa munthu, buwula. Buwula pamaso pawo ndi mtima wosweka ndi wachisoni chachikulu. Ndipo akadzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuwula?’ Iwe udzayankhe kuti, ‘Ndikubuwula chifukwa cha nkhani imene ndamva. Zikadzachitika zimenezi, mitima yonse idzangoti fumu, manja onse adzangolefuka, mpweya wawo udzawathera, ndipo mawondo onse adzangoti zii.’ Izi zikubwera! Ndipo zidzachitika ndithu, akutero Ambuye Yehova.”
Yehova anandiyankhulanso kuti, “Iwe mwana wa munthu, unenere ndipo unene kuti, Ambuye Yehova akuti,
“Izi ndi zimene Yehova akunena:
Lupanga, lupanga, lanoledwa ndipo lapukutidwa.
Lanoledwa kuti likaphe,
lapukutidwa kuti lingʼanime ngati mphenzi!
“ ‘Kodi tingakondwere bwanji? Wanyoza ndodo, mwana wanga ndi chilichonse cha mtengo.
“ ‘Lupanga laperekedwa kuti lipukutidwe,
ndi kuti linyamulidwe,
lanoledwa ndi kupukutidwa,
kuti liperekedwe mʼmanja mwa munthu amene amapha.
Fuwula ndi kulira, iwe mwana wa munthu,
pakuti zimenezi zidzagwera anthu anga;
zidzagweranso akalonga onse a Israeli.
Adzaphedwa ndi lupanga
pamodzi ndi anthu anga.
Chifukwa chake udzigugude pa chifuwa ndi chisoni.
“ ‘Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Ndikuwayesa anthu anga, ndipo ngati satembenuka mtima, ndiye kuti zimenezi sizidzalephera kuwagwera.’
“Tsono mwana wa munthu, nenera
ndipo uwombe mʼmanja.
Lupanga likanthe kawiri
ngakhale katatu.
Limenelo ndilo lupanga lophera anthu.
Inde ndilodi lupanga lophera anthu koopsa
limene likuwazungulira.
Ndawayikira pa zipata zawo zonse
lupanga laphuliphuli
kuti ataye mtima
ndiponso kuti anthu ambiri agwe.
Aa! Lapangidwa lupanga kuti lizingʼanima ngati mphenzi
ndi kuti azilisolola kuphera anthu.
Iwe lupanga, ipha anthu kumanja,
kenaka kumanzere,
kulikonse kumene msonga yako yaloza.
Inenso ndidzawomba mʼmanja mwanga,
ndipo ndidzaziziritsa ukali wanga
Ine Yehova ndayankhula.”
Yehova anandiyankhulanso kuti, “Iwe mwana wa munthu, ulembe zizindikiro za misewu iwiri imene lupanga la mfumu ya ku Babuloni lingathe kudzeramo. Misewu yonse ikhale yochokera mʼdziko limodzi. Ika chikwangwani pa mphambano yopita mu mzinda. Ulembe chizindikiro pa msewu umene lupanga lidzadzere popita ku Raba wa ku Amoni, ndiponso ku Yuda ndi ku Yerusalemu, mzinda wotetezedwa. Pakuti mfumu ya ku Babuloni yayima pa msewu, pa mphambano ya misewu iwiriyo. Ikuwombeza ndi mivi yake kuti idziwe njira yoyenera kudzeramo. Ikupempha nzeru kwa milungu yake ndipo ikuyangʼana chiwindi cha nyama yoperekedwa ku nsembe. Mʼdzanja lake lamanja muli muvi waula wolembedwa Yerusalemu. Kumeneko mfumuyo idzayika zida zogumulira, idzalamula kupha anthu ndiponso kufuwula mfuwu wa nkhondo. Mfumuyo idzapanga zida zogumulira makoma, kuwunda mitumbira ya nkhondo ndi kumanga nsanja za nkhondo. Koma kwa anthu a ku Yerusalemu zidzaoneka ngati zowombeza zabodza chifukwa cha malumbiro amene anachita kwa mfumuyo. Koma mfumuyo idzawakumbutsa za zolakwa zawo kuti atengedwe ku ukapolo.
“Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti, ‘Popeza mwandikumbutsa zolakwa, moti kundiwukira kwanu kwaonekera poyera ndi kuti mu zochita zanu zonse mukuonetsa machimo anu, nʼchifukwa chake mudzagwidwa ndi kutengedwa ukapolo.
“ ‘Tsono iwe kalonga wonyozedwa ndi woyipa wa Israeli, amene tsiku lako lafika, amene nthawi yako yolangidwa yafika penipeni, Ambuye Yehova akuti: Vula nduwira, chotsa chipewa chaufumu. Zinthu sizidzakhala monga zinalili: anthu wamba adzakwezedwa ndipo okwezedwa adzatsitsidwa. Chipasupasu! Chipasupasu! Ine ndidzawupasula mzindawo! Ndipo sadzawumanganso mpaka atafika amene ali woyenera kuwulandira; Ine ndidzawupereka kwa iyeyo.’
“Ndipo iwe mwana wa munthu, nenera kuti, ponena za Aamoni ndi zonyoza zawo, Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Lupanga, lupanga,
alisolola kuti liphe anthu,
alipukuta kuti liwononge
ndi kuti lingʼanime ngati mphenzi.
Zimene akuti akuona mʼmasomphenya zokhudza inu ndi zabodza.
Mawula awo okhudza inu ndi abodzanso.
Mudzakhala pamodzi ndi anthu oyipa
amene tsiku lawo lafika,
ndiye kuti nthawi
ya kulangidwa kwawo komaliza.
“ ‘Bwezerani lupanga mʼchimake.
Ku malo kumene inu munabadwira,
mʼdziko la makolo anu,
ndidzakuweruzani.
Ndidzakhuthula ukali wanga pa inu,
ndipo mkwiyo wanga udzakuyakirani.
Ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza;
anthu odziwa bwino kuwononga zinthu.
Mudzakhala ngati nkhuni pa moto.
Ena adzakhetsa magazi anu mʼdziko lanu lomwe.
Simudzakumbukiridwanso
pakuti Ine Yehova ndayankhula.’ ”
Machimo a Yerusalemu
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza mzinda uwo wa anthu akupha anzawo? Tsono uwudzudzule chifukwa cha machitidwe ake onse onyansa ndipo unene kuti, ‘Ambuye akuti: Iwe mzinda umene wadzigwetsa wekha mʼtsoka pa kukhetsa magazi pakati pako ndi kudziyipitsa popanga mafano, wapezekatu wolakwa chifukwa cha magazi amene wakhetsa, ndipo wadziyipitsa chifukwa cha mafano amene wapanga. Choncho wachepetsa masiku ako, ndipo zaka zako zafika kumapeto. Nʼchifukwa chake ndalola kuti anthu a mitundu ina akunyoze ndiponso kuti anthu a mayiko onse akuseke. Mayiko amene ali pafupi ndi mayiko omwe ali kutali adzakunyoza, iwe mzinda wa mbiri yoyipa, wodzaza ndi chiwawa.
“ ‘Taona momwe aliyense wa atsogoleri a Israeli amagwiritsira mphamvu zake kupha anthu. Mu mzindamo anthu amanyoza abambo ndi amayi awo. Iwo amapondereza alendo ndi kuzunza ana amasiye ndi akazi amasiye. Wanyoza zinthu zanga zopatulika ndi kuyipitsa Masabata anga. Mwa iwe muli anthu onenera anzawo zabodza kuti aphedwe. Mwa iwe mulinso amene amadyera zansembe pa mapiri a chipembedzo. Enanso amachita zonyansa. Mwa iwe muli ena ogonana ndi akazi a abambo awo, muli enanso amene amavuta akazi pamene ali woyipitsidwa ndi msambo. Ena amachita chigololo ndi akazi a anzawo, ndipo ena, mopanda manyazi, amayipitsa mkazi wa mwana wawo. Palinso ena amene amayipitsa alongo awo, ana aakazi a abambo awo. Mwa iwe muli anthu amene amalandira ziphuphu kuti aphe anzawo; ena amachita katapira ndi kupeza phindu loposera muyeso; enanso amapeza phindu mwachinyengo poopseza anzawo. Ndipo mwandiyiwala Ine, akutero Ambuye Yehova.
“ ‘Koma Ine ndachita kuwomba mʼmanja kuti phuu nʼkudabwa chifukwa cha phindu lachinyengo limene mwapeza ndiponso chifukwa cha kuphana kumene kumachitika pakati panu. Kodi mtima wako udzakhala wolimbabe kapena manja ako adzakhalabe amphamvu ndikadzatsiriza kukulanga iwe? Ine Yehova ndayankhula, ndipo ndidzazichitadi. Ndidzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukumwazirani ku mayiko onse. Umu ndi mmene ndidzachotsere zoyipa zako. Udzanyozedwa pamaso pa anthu a mitundu ina. Pambuyo pake udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, Aisraeli asanduka chinthu cha chabechabe kwa Ine. Onse ali ngati mkuwa, chitini, chitsulo ndi mtovu zotsala mʼngʼanjo atayeretsa siliva. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Pakuti nonse mwasanduka chinthu cha chabechabe, Ine ndidzakusonkhanitsani mu Yerusalemu. Monga momwe anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo, mtovu ndi chitini mʼngʼanjo ndi kusonkhetsa moto kuti azisungunule, motero Inenso ndidzakusonkhanitsani ndili wokwiya ndi waukali, ndipo ndidzakuyikani mʼkati mwa mzinda, ndikukusungunurani. Ndidzakusonkhanitsani mu mzindamo ndi kukoleza moto wa mkwiyo wanga, ndipo inu mudzasungunuka mu mzindamo. Monga siliva amasungunulidwa mʼngʼanjo, kotero inunso mudzasungunuka mʼkati mwa mzinda ndipo Inu mudzadziwa kuti Ine Yehova ndakukwiyirani.’ ”
Yehova anandiyankhulanso nati, “Iwe mwana wa munthu, uza dziko la Israeli kuti, ‘Iwe ndiwe dziko losayeretsedwa, ndiponso losavumbidwa ndi mvula chifukwa cha mkwiyo wanga.’ Atsogoleri ake mu mzindamo ali ngati mkango wobangula pogwira nyama. Apha anthu, alanda chuma ndi zinthu za mtengowapatali, ndiponso asandutsa amayi ambiri kukhala amasiye. Ansembe ake amaphwanya lamulo langa ndi kuyipitsa zinthu zanga zopatulika. Sasiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba. Saphunzitsa anthu kusiyana kwa zinthu zoyenera pa chipembedzo ndi zinthu zosayenera. Sasamalira za kusunga masabata anga. Motero Ine ndimanyozedwa pakati pawo. Atsogoleri ake ali ngati mimbulu yokhadzula nyama; amakhetsa magazi ndi kupha anthu kuti apeze phindu loyipa. Aneneri ake amabisa zonsezi monga muja amachitira anthu popaka njereza. Amazimphimba ndi zabodza zimene aona mʼmasomphenya awo ndi zonama za mʼmawula awo. Iwo amati, ‘Ambuye Yehova akuti,’ pamene Ine Yehova sindinayankhule. Anthu a mʼdzikomo amasautsa anzawo ndi kulanda anthu osowa. Amazunza anthu osauka ndi amphawi. Amavutitsa alendo posawachitira zinthu mwachilungamo.
“Ndinafunafuna munthu pakati pawo woti amange linga, woti ayimirire dziko pamaso panga kundipepesa kuti ndisaliwononge, koma sindinamupeze. Nʼchifukwa chake ndawakwiyira kwambiri. Ndawawonongeratu ndi mkwiyo wanga woyaka ngati moto. Ndawalanga molingana ndi zimene anachita. Akutero Ambuye Yehova.”
Za Yerusalemu ndi Samariya
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, panali atsikana awiri ana a mayi mmodzi. Iwo ankachita za chiwerewere ku Igupto. Za chiwerewerezo anayamba ali achichepere. Kumeneko anthu ankangowasisita pa chifuwa ndi kuwagwiragwira mawere awo aja. Wamkulu dzina lake anali Ohola, ndipo mngʼono wakeyo anali Oholiba. Ine ndinawakwatira ndipo anabereka ana aamuna ndi ana aakazi. Ohola ndiye Samariya, ndipo Yerusalemu ndiye Oholiba.
“Ohola anachita zachiwerewere ngakhale anali mkazi wanga; ndipo iye anakangamira abwenzi ake a ku Asiriya. Amenewo anali asilikali ovala zibakuwa zamlangali, abwanamkubwa ndiponso atsogoleri a nkhondo. Onsewo anali anyamata osiririka ndipo ankakwera pa akavalo. Ohola anachita zachiwerewere ndi onsewa, anthu otchuka a ku Asiriya. Iye anadziyipitsa ndi mafano a munthu aliyense amene anagona naye. Iye sanaleke za chiwerewere zimene anaziphunzira ku Igupto. Paja akanali mtsikana anyamata ankagona naye. Iwo ankamusisita mawere akanali anthete nachita naye zachiwerewere.
“Nʼchifukwa chake Ine ndinamupereka kwa achikondi ake, Asiriya, amene iye ankawalakalaka. Iwowa anamuvula, namulanda ana ake aamuna ndi aakazi ndipo anamupha ndi lupanga. Ndipo atalangidwa choncho, iye anasanduka chinthu chonyozeka pakati pa akazi.
“Mphwake Oholiba anaona zimenezi natengerako. Koma iye anachita zachiwerewere kuposa mkulu wake. Iyenso anakangamira Asiriya, abwanamkubwa, olamulira asilikali, ankhondo ovala zovala zonse za nkhondo ndi okwera pa akavalo. Onsewa anali anyamata osiririka. Ndinaona kuti iyenso anadziyipitsa; ndipo onse awiriwo anatsata njira imodzi.
“Koma Oholiba uja anachita chigololo kopitirira mkulu wake. Iye anaona zithunzi za amuna pa khoma, zithunzi za Ababuloni zolembedwa ndi inki yofiira, atamanga malamba mʼchiwuno mwawo ndi kuvala nduwira pa mitu yawo. Onse amaoneka ngati atsogoleri a magaleta a Ababuloni, mbadwa za ku Kaldeya. Oholiba atangowaona, anawalakalaka ndipo anatuma amithenga ku Kaldeya kukawayitana. Ndipo Ababuloni anabwera nʼkudzagona naye. Choncho mwa chilakolako chawo anamuyipitsa. Koma atamuyipitsa choncho, iye ananyansidwa nawo. Iye atachita chiwerewere chake poyera ndi kuonetsa umaliseche wake, Ine ndinamuchokera monyansidwa monga mmene ndinachitira ndi mʼbale wake. Koma anachitabe zachiwerewere osalekeza. Ankakumbukira masiku a ubwana wake pamene ankachita za chiwerewere mʼdziko la Igupto. Kumeneko iye ankalakalaka zibwenzi zake, amene ziwalo zawo zinali ngati za abulu ndipo kutentha kwawo kunali ngati kwa akavalo. Motero, iwe Oholiba unafuna kuchitanso zadama monga unkachitira ku Igupto pamene unali mtsikana. Nthawi imene ija ankakusisita pa chifuwa ndi kugwiragwira mawere ako osagwa aja.
“Tsono iwe Oholiba, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakudzutsira zibwenzi zako zimene unkanyansidwa nazo zija kuti zilimbane nawe. Ndidzaziyitana kuti zibwere kuchokera mbali zonse. Ndidzayitana anthu a ku Babuloni ndi Akaldeya onse, anthu a ku Pekodi, Sowa ndi Kowa pamodzi ndi Asiriya onse. Onsewa ndi amuna osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri a ankhondo, oyenda pa magaleta, anthu a maudindo akuluakulu. Onsewa ndi okwera akavalo. Iwo adzabwera kudzalimbana nawe ndi zida za nkhondo, magaleta ndi ngolo, pamodzi ndi anthu ambiri. Adzakuzinga mbali zonse atavala zishango zankhondo ndi zipewa zankhondo. Ndidzakupereka kwa iwo kuti akulange ndipo adzakulanga monga momwe adzafunire. Ndidzaonetsa mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga iwe mwankhanza. Adzadula mphuno zanu ndi makutu anu, ndipo amene adzatsalira mwa iwe adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzakulanda ana ako aamuna ndi aakazi ndipo amene adzatsalira adzaphedwa ndi moto. Adzakuvulaninso zovala zanu ndikukulandani zodzikongoletsera zanu zamtengowapatali. Motero ndidzathetsa zonyansa zako ndi zachigololo zomwe unaziyamba ku Igupto. Choncho sudzalakalaka za ku Igupto kapena kuzikumbukiranso.
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikukupereka mʼmanja mwa amene amadana nawe, kwa iwo amene unawafulatira moyipidwa nawo. Adzachita nawe mwachidani. Adzakulanda zonse zimene unagwirira ntchito. Adzakusiya wamaliseche ndiponso wausiwa. Kuyipa kwa makhalidwe ako achiwerewere kudzakhala pammbalambanda. Zonyansa zako ndi chiwerewere chako, zabweretsa izi pa iwe chifukwa unachita zonyansa ndi anthu a mitundu ndi kudziyipitsa ndi mafano awo. Unatsata zochita za mkulu wako; choncho Ine ndidzayika chikho cha chilango chake mʼdzanja lako.
“Ine Ambuye Yehova ndikuti:
“Udzamwera chikho cha mkulu wako,
chikho chachikulu ndi chakuya;
anthu adzakuseka ndi kukunyoza,
pakuti chikhocho ndi chodzaza kwambiri.
Udzaledzera ndipo mtima wako udzadzaza ndi chisoni.
Chimenechi ndi chikho chachiwonongeko ndi chipasupasu,
chikho cha mkulu wako Samariya.
Udzamwa chikhocho mpaka kugugudiza.
Tsono udzaphwanyaphwanya chikhocho
ndipo udzangʼamba mawere ako ndi zigoba zake.
Ine ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.
“Chifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza wandiyiwala Ine ndi kundifulatira, chomwecho uyenera kulangidwa chifukwa cha zonyansa zako ndi chiwerewere chako.”
Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi udzaweruza Ohola ndi Oholiba? Tsono uwayimbe mlandu chifukwa cha machitidwe awo onyansa. Iwo achita chigololo ndipo anapha anthu. Anachita chigololo popembedza mafano awo. Ngakhale ana amene anandiberekera Ine anawapereka kwa mafanowo ngati chakudya chawo. Anachitanso izi: Iwo anayipitsa malo anga opatulika ndi kudetsa masabata anga. Atapereka ana awo kwa mafano, tsiku lomwelo anakalowanso mʼNyumba yanga yopatulika ndi kuyipitsamo. Izi ndi zimene anachita mʼNyumba mwanga.
“Iwo anatuma amithenga kukayitana amuna a ku mayiko akutali. Anthuwo atabwera, abale awiri aja anasambasamba, kudzola utoto wodzikometsera kumaso, kenaka ndi kuvala zovala zamakaka. Anakhala pa bedi lokongola ndipo patsogolo pawo panali tebulo pamene munayikapo lubani ndi mafuta. Zonse zowapatsa Ine.
“Mfuwu wa chigulu cha anthu unamveka. Anthu oledzera ochokera ku chipululu anabwera pamodzi ndi anthu wamba ndipo anaveka akaziwo zibangiri kumanja ndi zipewa zaufumu zokongola ku mutu. Ndipo ine ndinati za mkazi wotheratu ndi chigololoyo, ‘Tsono asiyeni kuti achite naye monga wachiwerewere, pakuti ichi ndi chimene iye ali basi.’ Tsono anapita kwa iwo monga mmene anthu amapitira kwa mkazi wadama. Momwemo anapita kwa Ohola ndi kwa Oholiba kukachita nawo zadama. Koma anthu olungama adzawazenga anthuwa mlandu wa chigololo ndi wa kupha anthu. Ndi iwodi anthu achigololo ndiponso mʼmanja mwawo muli magazi.
“Ambuye Yehova akuti: Itanitsani chigulu cha anthu kuti chidzawalange ndi kulanda chuma chawo. Anthuwo adzawaponye miyala akazi awiriwo ndi kuwatema ndi malupanga awo. Ana awo aamuna ndi aakazi adzawaphe ndi kutentha nyumba zawo.
“Motero Ine ndidzathetsa zachigololo mʼdzikomo, ndipo akazi onse adzatengapo phunziro kuti asadzachite zachigololo monga za iwowo. Ndidzawalanga chifukwa cha ntchito zawo za dama ndipo adzazunzika chifukwa cha tchimo lawo lopembedza mafano. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.”
Mʼphika Wophikira
Pa tsiku lakhumi la mwezi wakhumi chaka chachisanu ndi chinayi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu lemba dzina la tsiku lalero, lero lomwe lino, chifukwa mfumu ya Babuloni yazungulira Yerusalemu lero lino. Uwaphere mwambi anthu owukirawa ndi kuwawuza kuti: ‘Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Ikani mʼphika pa moto,
ndipo mu mʼphikamo muthiremo madzi.
Mu mʼphikamo muyikemo nthuli za nyama,
nthuli zonse zabwino kwambiri za mwendo wathako ndi mwendo wamwamba.
Mudzadzemo mafupa abwino kwambiri.
Pa gulu la nkhosa musankhepo nkhosa yabwino kwambiri.
Muyike nkhuni pansi pa mʼphikawo.
Madzi awire.
Kenaka muphike nyamayo pamodzi ndi mafupa omwe.’
“ ‘Nʼchifukwa chake, Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi,
tsoka kwa mʼphika wadzimbiri;
dzimbiri lake losachoka!
Mutulutsemo nthuli imodzimodzi
osasankhulapo.
“ ‘Paja magazi amene anakhetsa akanali pakati pake mu mzindamo.
Iye awakhuthulira pa thanthwe losalala.
Sanawakhutulire pa dothi
kuopa kuti fumbi lingawafotsere.
Ndinasiya magaziwo pa mwala wosalala
kuti asafotseredwe ndi fumbi
chifukwa ndinafuna kuonetsa mkwiyo wanga ndi kulipsira.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:
“ ‘Tsoka kwa mzinda wokhetsa magazi!
Inenso, ndidzawunjika mulu waukulu wa nkhuni.
Choncho wonjeza nkhuni
ndipo muyatse moto.
Phikani nyamayo bwinobwino,
muthiremo zokometsera,
mutsanule msuzi, ndipo mupsereze mafupawo.
Tsono muyike pa makala mʼphika wopanda kanthuwo
mpaka utenthe kuchita kuti psuu
kuti zonyansa zake zisungunuke
ndi kuti dzimbiri lake lichoke.
Koma mʼphikawo walephereka kuyeretsedwa.
Dzimbiri lake linalowerera silingatheke kuchoka
ngakhale ndi moto womwe.
“ ‘Tsono dzimbiri limeneli ndi zilakolako za dama lako. Pakuti ine ndinayesa kukutsuka koma iwe sunayere, ndipo sudzayeranso mpaka ukali wanga utakwaniratu pa iwe.
“ ‘Ine Yehova ndayankhula. Zimenezi zikubwera ndipo ndidzazichitadi. Sindidzabwerera mʼmbuyo. Sindidzakulekerera kapena kukuchitira chifundo. Ndidzakulanga molingana ndi makhalidwe ndi machitidwe ako, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Imfa ya Mkazi wa Ezekieli
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, Ine ndikulanda mwadzidzidzi mkazi amene amakukomera mʼmaso kwambiri. Koma usadandaule, usalire kapena kukhetsa misozi. Ubuwule koma mwakachetechete. Usamulire wakufayo. Uvale nduwira yako ndithu, nsapato zakonso usavule. Usaphimbe nkhope kapena kudya chakudya cha anamfedwa.”
Choncho ndinayankhula ndi anthu mmawa, ndipo madzulo mkazi wanga anamwalira. Mmawa mwake ndinachita monga momwe anandilamulira.
Ndipo anthu anandifunsa kuti, “Kodi sutifotokozera tanthauzo la zimene ukuchitazi?”
Ndinawayankha kuti, “Yehova anandipatsa uthenga wakuti, ‘Awuze Aisraeli kuti: Ine Ambuye Yehova ndikuti: ndidzayipitsa Nyumba yanga yopatulika, nyumba imene mwakhala mukuyinyadira. Mumakondwa kwambiri poyiona, ndipo mumayikonda ndi mtima onse. Ana aamuna ndi aakazi amene munawasiya mʼmbuyo adzaphedwa ndi lupanga. Ndipo mudzachita monga ndachitira inemu. Inu simudzaphimba nkhope zanu kapena kudya chakudya cha anamfedwa. Mudzavala nduwira zanu kumutu ndi nsapato zanu ku mapazi anu. Simudzabuma maliro kapena kukhetsa misozi koma mudzavutika kwambiri chifukwa cha machimo anu ndipo mudzabuwula pakati panu. Ine Ezekieli ndidzakhala chitsanzo chanu. Mudzachita monga momwe ndachitira. Izi zikadzachitika, akutero Yehova, ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Wamphamvuzonse.’
“Ndipo Yehova anandiyankhula nati: Iwe mwana wa munthu, tsiku lina ndidzawachotsera anthuwa linga lawo limene ankakondwerera kukongola kwake, limene linkawakomera mʼmaso mwawo, limenenso anayikapo mtima wawo kwambiri. Ndidzawachotsera ana awo aamuna ndi aakazi. Pa tsiku limenelo wothawa nkhondo adzabwera kudzakuwuzani zimenezo. Pa tsiku limenelo pakamwa pako padzatsekuka. Udzatha kuyankhula naye ndipo sudzakhalanso chete. Motero udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Za Chilango cha Aamoni
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira anthu a ku Amoni ndipo unenere mowadzudzula. Awawuze kuti, ‘Inu anthu a ku Amoni, imvani zimene Ambuye Yehova akunena. Iye akuti: Inu munanena mawu onyoza pamene Nyumba yanga yopatulika inkayipitsidwa. Munanyozanso dziko la Israeli pamene linaguga ndiponso anthu a ku Yuda pamene anatengedwa ukapolo. Nʼchifukwa chake Ine ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu akummawa ngati cholowa chawo. Iwo adzamanga misasa yawo ndi kukhoma matenti awo pakati panu. Adzadya zipatso zanu ndi kumwa mkaka wanu. Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira ndi mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Zimene ndikunena Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu munawomba mʼmanja ndi kumalumphalumpha. Munkakondwa mu mtima mwanu pamene munkanyoza dziko la Israeli. Nʼchifukwa chake ndidzatambasula dzanja langa kuti ndikulangeni, ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha anthu a mitundu ina. Ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukufafanizani mʼmayiko onse. Ndidzakuwonongani, ndipo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova!’ ”
Za Chilango cha Mowabu
“Ambuye Yehova akuti, ‘Anthu a ku Mowabu ndi a ku Seiri ananena kuti anthu a ku Yuda ali ngati mayiko ena onse.’ Nʼchifukwa chake ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, kuyambira ku mizinda yake ya kumalire; mizinda yokongola ya Beti-Yesimoti, Baala-Meoni ndi Kiriataimu. Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni mʼmanja mwa anthu akummawa kotero kuti Aamoni adzayiwalikiratu pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzawalangadi Amowabuwo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Za Chilango cha Edomu
“Ambuye Yehova akuti, ‘Pakuti Edomu analipsira Ayuda, ndiye kuti analakwa kwambiri pochita zimenezi. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kulanga Edomu ndi kupha anthu ake ndiponso nyama zawo. Ndidzawonongeratu Edomu ndipo adzaphedwa ndi lupanga kuchokera ku Temani mpaka ku Dedani. Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraeli. Adzalanga anthu a ku Edomu molingana ndi mkwiyo ndi ukali wanga. Choncho adzaona kulipsira kwanga akutero Ambuye Yehova.’ ”
Za Chilango cha Filisitiya
“Ambuye Yehova akuti, ‘Afilisti analanga anthu anga mwankhanza ndi kuwalipsira. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzatambasula dzanja langa kukantha Afilistiwo. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga iwo amene amakhala mʼmbali mwa nyanja. Ndidzawabwezera chilango choopsa ndipo ndidzawalanga mu mkwiyo wanga. Ndikadzawalipsira ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Za Chilango cha Turo
Pa chaka cha khumi ndi chimodzi, tsiku loyamba la mwezi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Turo ananyogodola Yerusalemu kuti ‘Hii! Uja amene anali chipata choloweramo anthu a mitundu ina wawonongeka. Zitseko zake zatsekukira ife. Tidzalemera popeza wasanduka bwinja.’ Nʼchifukwa chake, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzakulangani, inu anthu a ku Turo. Ndidzakuyitanirani anthu a mitundu ina kuti adzakulangeni monga momwe mafunde amawombera pa Nyanja. Anthuwo adzawononga makoma a Turo ndi kugwetsa nsanja zake. Ndidzapala dothi lake ndipo ndidzamusandutsa thanthwe losalala. Udzakhala poyanikapo makoka pakati pa nyanja. Ine Ambuye Yehova ndayankhula zimenezo. Udzasanduka chofunkha cha anthu a mitundu ina. Anthu okhala ku mtunda adzasakazidwa ndi lupanga. Pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Iwe Turo, ndidzakubweretsera Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni mfumu ya mafumu, kuchokera kumpoto pamodzi ndi akavalo ndiponso magaleta, anthu okwera pa akavalo ndi gulu lalikulu la ankhondo. Anthu okhala ku mtunda adzawapha ndi lupanga. Adzapanga mitumbira yankhondo ndi kukukwezera zishango kuti alimbane nawe. Adzagwetsa makoma ako ndi zida zogumulira khoma ndi kugwetsa nsanja zako ndi nkhwangwa zake. Akavalo ake adzakhala ochuluka kwambiri kotero kuti adzakukwirira ndi fumbi lawo. Makoma ako adzagwedezeka ndi mdidi wa akavalo, ngolo ndi magaleta pamene iye adzalowa pa zipata monga mmene amalowera mu mzinda umene makoma ake agwetsedwa. Akavalo ake adzapondaponda mʼmisewu yako yonse ndi ziboda zawo. Adzapha anthu ako ndi lupanga. Mizati yako yolimba idzagwetsedwa. Iwo adzafunkha chuma chako ndipo adzalanda zinthu zako za malonda. Adzagwetsa makoma ako ndi kuwononga nyumba zako zabwino. Adzaponya miyala yako, matabwa ako ndi dothi lako mʼnyanja. Choncho ndidzathetsa phokoso la nyimbo zanu, ndipo kulira kwa apangwe ako sikudzamvekanso. Ndidzakusandutsa thanthwe losalala, ndipo udzakhala malo woyanikapo makoka a nsomba. Sudzamangidwanso, pakuti Ine Yehova ndayankhula, akutero Ambuye Yehova.
“Ine Ambuye Yehova ndikukuwuza, iwe mzinda wa Turo, kuti zilumba zidzagwedezeka pakumva za kugwa kwako ndiponso poona anthu opweteka akubuwula ndipo anthu akuphedwa pakati pako. Pamenepo mafumu a mʼmbali mwa nyanja adzatsika pa mipando yawo yaufumu. Adzayika pambali mikanjo yawo ndi kuvala zovala zawo zamakaka. Adzachita mantha ndipo adzakhala pansi akunjenjemera kosalekeza. Adzathedwa nzeru poona zimene zakugwera. Pamenepo adzayimba nyimbo yokudandaula ndipo adzati kwa iwe:
“ ‘Nʼkuchita kuwonongeka chotere, iwe mzinda wotchuka,
wodzaza ndi anthu a ku nyanja!
Unali wamphamvu pa nyanja,
iwe ndi nzika zako;
unkaopseza anthu onse amene
ankakhala kumeneko.
Tsopano mayiko a mʼmbali mwa nyanja akunjenjemera
chifukwa cha kugwa kwako;
okhala pa zilumba nawonso agwidwa ndi mantha aakulu
chifukwa cha kugwa kwako.’
“Mawu a Ine Ambuye Yehova ndi awa: Ndidzakusandutsa bwinja, ngati mizinda imene anthu sangathe kukhalamo. Ndidzakuphimba ndi madzi ozama a mʼnyanja, madzi amphamvu woti akumize. Ndidzakugwetsa pansi kuti ukhale pamodzi ndi anthu amvulazakale amene akutsikira ku manda. Ine ndidzakusunga ku dzenjeko ngati ku bwinja losiyidwa kalekale, pamodzi ndi anthu amene anafa kale motero sudzabwererako kukhala pakati pa anthu amoyo. Ine ndidzakuthetsa mochititsa mantha, ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna, koma sudzapezekanso, akutero Ambuye Yehova.”
Nyimbo Yodandaulira Turo
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira Turo. Uza Turo, mzinda wokhala pa dooko la nyanja, wochita malonda ndi anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja kuti: Ambuye Yehova akuti,
“Iwe Turo, umanena kuti,
‘Ndine wokongola kwambiri.’
Malire ako anali mʼkati mwenimweni mwa nyanja;
amisiri ako anakukongoletsa kwambiri.
Anakupanga ndi matabwa
a payini ochokera ku Seniri;
anatenga mikungudza ya ku Lebanoni
kupangira mlongoti wako.
Ndi mitengo ya thundu ya ku Basani
anapanga zopalasira zako;
ndi matabwa a mitengo ya payini yochokera ku zilumba za Kitimu.
Pakuti anapanga thandala lako pakati pa matabwawo panali minyanga ya njovu.
Nsalu yabafuta yopeta yochokera ku Igupto inali thanga yako,
ndipo inakhala ngati mbendera.
Nsalu zophimba matenti ako zinali za mtundu wamtambo ndi pepo
zochokera ku zilumba za Elisa.
Anthu a ku Sidoni ndi Arivadi ndi amene anali opalasa ako.
Anthu aluso ako, iwe Turo, anali mwa iwe ndiwo amene ankakuyendetsa.
Akuluakulu ndi eni luso a ku Gebala anali mʼkati mwako,
ngati okonza zibowo zako.
Sitima za pa nyanja zonse, ndi oyendetsa ake
ankabwera pamodzi ndi katundu kudzachita nawe malonda.
“Anthu a ku Perisiya, a ku Ludi ndi Puti
anali asilikali mʼgulu lako la nkhondo.
Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo zankhondo pa makoma ako,
kubweretsa kwa iwe ulemerero.
Anthu a ku Arivadi ndi Heleki
ankalondera mbali zonse za mpanda wako;
anthu a ku Gamadi
anali mu nsanja zako,
Iwo ankapachika zishango zawo pa makoma ako onse.
Amenewo ndiwo anakukongoletsa kwambiri.
“Dziko la Tarisisi linachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa katundu wako wamtundumtundu. Iwo ankapereka siliva, chitsulo, chitini ndi mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Yavani, Tubala ndi Mesaki ankachita nawe malonda; iwo ankapereka akapolo ndi ziwiya za mtovu mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Anthu a ku Beti Togarima ankapereka akavalo antchito, akavalo ankhondo ndi abulu mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Anthu a ku Dedani ankachita nawe malonda, ndipo anthu ambiri a mʼmbali mwa nyanja anali ogula malonda ako. Ankakupatsa minyanga ya njovu ndi phingo.
“Anthu a ku Aramu ankachita nawe malonda chifukwa cha kuchuluka kwa zinthu zako. Iwo ankapereka miyala ya emeradi, nsalu zapepo, nsalu zopetapeta, nsalu zabafuta, korali ndi miyala ya rubi mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Yuda ndi Israeli ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka tirigu ochokera ku Miniti ndi zokometsera zakudya, uchi, mafuta ndi mankhwala mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Anthu a ku Damasiko, chifukwa cha zinthu zako za malonda zambiri ndi katundu wako wosiyanasiyana, ankachita nawe malonda a vinyo wochokera ku Heliboni ndi ubweya wankhosa ochokera ku Zahari. Adani ndi Agriki ochokera ku Uzala ankagula katundu wako. Iwo ankapereka chitsulo chosalala, kasiya ndi bango lonunkhira mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Anthu a ku Dedani ankakugulitsa nsalu zoyika pa zishalo za akavalo.
“Arabiya ndi mafumu onse a ku Kedara anali ogula malonda ako. Iwo ankachita nawe malonda a ana ankhosa onenepa, nkhosa zazimuna ndi mbuzi.
“Anthu amalonda a ku Seba ndi Raama ankachita nawe malonda. Iwo ankapereka zonunkhira zosiyanasiyana zabwino kwambiri, miyala yokongola ndi golide mosinthanitsa ndi katundu wako.
“Amalonda a ku Harani, Kane, Edeni, Seba, Asuri ndi Kilimadi ankachita nawe malonda. Iwowa ankasinthanitsana nawe zovala zokongola, nsalu zopetapeta, zoyala pansi za mawangamawanga, atazimanga bwino ndi zingwe zolimba.
“Sitima za pa madzi za ku Tarisisi zinali
zonyamula malonda ako.
Motero iwe uli ngati sitima yapamadzi
yodzaza ndi katundu wolemera.
Anthu opalasa ako amakupititsa
pa nyanja yozama.
Koma mphepo yakummawa idzakuthyolathyola
pakati pa nyanja.
Chuma chako, katundu wako, malonda ako,
okuyendetsa ako, okuwongolera ako ndi opanga sitima za pa madzi,
anthu ako amalonda ndi asilikali ako onse
ndiponso aliyense amene ali mʼmenemo
adzamira mʼnyanja
tsiku limene udzawonongeka.
Madera a mʼmbali mwa nyanja adzagwedezeka
chifukwa cha kufuwula kwa oyendetsa sitimawo.
Onse amene amapalasa sitima zapamadzi,
adzatuluka mʼsitima zawo;
oyendetsa ndi onse owongolera sitima zapamadzi
adzayimirira mʼmbali mwa nyanja.
Iwo akufuwula,
kukulira iwe kwambiri;
akudzithira fumbi kumutu,
ndi kudzigubuduza pa phulusa.
Akumeta mpala mitu yawo chifukwa cha iwe
ndipo akuvala ziguduli.
Akukulira iweyo
ndi mitima yowawa kwambiri.
Akuyimba nyimbo
yokudandaulira nʼkumati:
‘Ndani anawonongedwapo ngati Turo
pakati pa nyanja?’
Pamene malonda ako ankawoloka nyanja
unakhutitsa mitundu yambiri ya anthu.
Mafumu a dziko lapansi analemera ndi chuma chako
komanso ndi malonda ako.
Koma tsopano wathyokera mʼnyanja,
pansi penipeni pa nyanja.
Katundu wako ndi onse amene anali nawe
amira pamodzi nawe.
Onse amene amakhala mʼmbali mwa nyanja
aopsedwa ndi zimene zakuchitikira.
Mafumu awo akuchita mantha
ndipo nkhope zangoti khululu.
Anthu amalonda a mitundu ina akukunyogodola.
Watha mochititsa mantha
ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.”
Mawu Odzudzula Mfumu ya Turo
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, iwuze mfumu ya ku Turo mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Iwe ndi mtima wako wodzikuza
umanena kuti, ‘Ine ndine mulungu;
ndimakhala pa mpando wa mulungu
pakati pa nyanja.’
Koma ndiwe munthu chabe osati mulungu,
ngakhale ukuganiza kuti ndiwe wanzeru ngati mulungu.
Taona, ndiwedi wanzeru kupambana Danieli.
Ndipo palibe chinsinsi chobisika kwa iwe.
Mwa nzeru zako ndi kumvetsa kwako
unadzipezera chuma
ndipo unasonkhanitsa golide ndi siliva
mʼnyumba zosungira chuma chako.
Ndi nzeru zako zochitira malonda
unachulukitsa chuma chako
ndipo wayamba kunyada
chifukwa cha chuma chakocho.
“ ‘Choncho Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Popeza umadziganizira
kuti ndiwe mulungu,
Ine ndidzabwera ndi anthu achilendo, anthu ankhanza,
kuti adzalimbane nawe.
Adzakuthira nkhondo kuti awononge zonse zimene unazipeza ndi nzeru zako,
ndipo adzawononga kunyada kwakoko.
Iwo adzakuponyera ku dzenje
ndipo udzafa imfa yoopsa
mʼnyanja yozama.
Kodi udzanenabe kuti, ‘Ine ndine mulungu,’
pamaso pa iwo amene akukupha?
Iwe udzaoneka kuti ndiwe munthu chabe, osati mulungu,
mʼmanja mwa iwo amene akukuphawo.
Udzafa imfa ya anthu osachita mdulidwe
mʼmanja mwa anthu achilendo.
Ine ndayankhula zimenezi, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yodandaulira mfumu ya Turo ndipo uyiwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti,
“ ‘Iwe unali chitsanzo cha ungwiro weniweni,
wodzaza ndi nzeru ndi wokongola kwambiri.
Iwe unkakhala ngati mu Edeni,
munda wa Mulungu.
Miyala yokongola ya mitundu yonse:
rubi, topazi ndi dayimondi,
kirisoliti, onikisi, yasipa,
safiro, kalineliyoni ndi berili ndiwo inali zofunda zako.
Ndipo zoyikamo miyalayo zinali zagolide.
Anakupangira zonsezi pa tsiku limene unalengedwa.
Ndinayika kerubi kuti azikulondera.
Unkakhala pa phiri langa lopatulika,
ndipo unkayendayenda
pakati pa miyala ya moto.
Makhalidwe ako anali abwino
kuyambira pamene unalengedwa
mpaka nthawi imene unayamba kuchita zoyipa.
Unatanganidwa ndi zamalonda.
Zotsatira zake zinali zoti unachulukitsa zandewu
ndi kumachimwa.
Choncho ndinakuchotsa ku phiri langa lopatulika.
Mkerubi amene ankakulondera uja anakupirikitsa
kukuchotsa ku miyala yamoto.
Unkadzikuza mu mtima mwako
chifukwa cha kukongola kwako,
ndipo unayipitsa nzeru zako
chifukwa chofuna kutchuka.
Kotero Ine ndinakugwetsa pansi
kuti ukhala chenjezo pamaso pa mafumu.
Ndi malonda ako achinyengo unachulukitsa machimo ako.
Motero unayipitsa malo ako achipembedzo.
Choncho ndinabutsa moto pakati pako,
ndipo unakupsereza,
ndipo unasanduka phulusa pa dziko lapansi
pamaso pa anthu onse amene amakuona.
Anthu onse amitundu amene ankakudziwa
akuchita mantha chifukwa cha iwe.
Watheratu mochititsa mantha
ndipo sudzakhalaponso mpaka muyaya.’ ”
Za Chilango cha Sidoni
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu, utembenukire ku mzinda wa Sidoni ndipo unenere mowudzudzula kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndine mdani wako, iwe Sidoni,
ndipo ndidzalemekezedwa chifukwa cha iwe.
Anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova
ndikadzakulanga ndi kudzionetsa kuti
ndine woyera pakati pako.
Ndidzatumiza mliri pa iwe
ndi kuchititsa magazi kuti ayende mʼmisewu yako.
Anthu ophedwa ndi lupanga
adzagwa mbali zonse.
Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Nthawi imeneyo Aisraeli sadzakhalanso ndi anthu pafupi achipongwe amene ali ngati nthula zowawa ndi ngati minga zopweteka. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.
“ ‘Ine Ambuye Yehova mawu anga ndi awa: Nditasonkhanitsa Aisraeli kuchoka ku mayiko kumene anamwazikira, ndidzadzionetsa kuti ndine woyera pakati pawo pamaso pa anthu a mitundu ina. Adzakhala mʼdziko lawo, limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo. Adzakhala kumeneko mwamtendere ndipo adzamanga nyumba ndi kulima minda ya mpesa. Adzakhala kumeneko mwamtendere pamene ndidzalange anthu oyandikana nawo, amene ankawanyoza. Motero iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo.’ ”
Za Chilango cha Igupto
Pa tsiku lakhumi ndi chiwiri la mwezi wakhumi, chaka chakhumi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Farao, mfumu ya Igupto, ndipo unenere modzudzula mfumuyo pamodzi ndi dziko lake. Uyiwuze mfumuyo kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndine mdani wako, iwe Farao mfumu ya Igupto,
iwe ngʼona yayikulu yogona pakati pa mitsinje yako.
Umanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga;
ndinadzipangira ndekha.’
Koma ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako
ndipo nsomba za mʼmitsinje yako zidzakangamira ku mamba ako.
Tsono ndidzakutulutsa mu mtsinje mwakomo
pamodzi ndi nsomba zimene zakangamira ku mamba ako.
Ndidzakutaya ku chipululu,
iwe pamodzi ndi nsomba zonse za mʼmitsinje yako.
Udzagwera pamtetete kuthengo
popanda munthu woti akutole kuti akayike maliro ako.
Ndidzakusandutsa chakudya
cha zirombo za pa dziko lapansi ndi mbalame za mlengalenga.
Motero aliyense amene amakhala mu Igupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Iwe unakhala ngati ndodo yabango ku Aisraeli. Pamene anakugwira unathethekera mʼmanja mwawo ndi kucheka mapewa awo. Pamene anakutsamira, unathyoka ndipo misana yawo inagwedezeka.
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, ndikubweretsera lupanga kuti lidzaphe anthu pamodzi ndi nyama zomwe. Dziko la Igupto lidzasanduka lopanda anthu. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Popeza iwe unati, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga; ndinawupanga ndine,’ nʼchifukwa chake Ine ndikudana nawe pamodzi ndi mitsinje yakoyo, ndipo ndidzasandutsa dziko la Igupto bwinja kuyambira chipululu cha Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani, kukafika ku malire a Kusi. Palibe phazi la munthu kapena la nyama limene lidzapondepo. Kudzakhala kopanda anthu kwa zaka makumi anayi. Ndidzasandutsa dziko la Igupto kukhala chipululu ngati zipululu za mayiko ena. Kwa zaka makumi anayi mizinda yakenso idzakhala yopasuka pakati pa mizinda yopasuka. Ndipo ndidzathamangitsira Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndi kuwabalalitsira mʼmayiko.
“ ‘Komabe Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pakutha pa zaka makumi anayi ndidzasonkhanitsa Aigupto onse kuchokera ku mayiko amene ndinawabalalitsirako. Ndidzachotsa Aiguptowo ku ukapolo ndipo ndidzawabwezera ku Patirosi kumene anachokera. Kumeneko iwo adzakhala ufumu wotsika. Udzakhala ufumu wotsika kwambiri kupambana maufumu ena onse ndipo sudzadzitukumula pakati pa mitundu ina. Ndidzawufowoketsa kwambiri kotero kuti sudzathanso kulamulira mitundu ya anthu. Aisraeli sadzadaliranso Aigupto. Koma kuti chilango chawo chidzawakumbutsa tchimo lawo lija lofunafuna thandizo kuchokera ku Igupto. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.’ ”
Mphotho ya Nebukadinezara
Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, chaka cha 27, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, kale Nebukadinezara mfumu ya Babuloni inagwiritsa ntchito ankhondo ake kukathira nkhondo mzinda wa Turo, mpaka munthu aliyense anachita dazi chifukwa chosenza katundu, ndipo ananyuka pa phewa. Komabe ngakhale iyeyo, kapena gulu lake lankhondo sanaphulepo kanthu pa ntchito yonse imene anayigwira polimbana ndi mzindawo. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndidzapereka Igupto kwa Nebukadinezara mfumu ya Babuloni, ndipo iyo idzatenga chuma chake ndi kuchifunkha ngati malipiro a gulu lake lankhondo. Ndamupatsa Nebukadinezara Igupto ngati mphotho ya kulimbika kwake chifukwa iyo ndi gulu lake lankhondo anandigwirira ntchito, akutero Ambuye Yehova.
“Pa nthawi imeneyo ndidzapereka mphamvu yatsopano pa Aisraeli, ndipo ndidzatsekula pakamwa pako, iwe, Ezekieli kuti uthe kuyankhula pakati pawo. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Za Kulangidwa kwa Igupto
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, nenera ndipo ulengeze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena.
“ ‘Ufuwule mawu awa akuti,
‘Kalanga, tsiku lafika!’
Pakuti tsiku layandikira,
tsiku la Yehova lili pafupi,
tsiku la mitambo yakuda,
tsiku lachiwonongeko cha mitundu ya anthu.
Lupanga lidzabwera kudzalimbana ndi Igupto
ndipo mavuto adzafika pa Kusi.
Pamene anthu ambiri adzaphedwa mu Igupto,
chuma chake chidzatengedwa
ndipo maziko ake adzagumuka.
Kusi, Puti, Ludi ndi Arabiya yense, Libiya ndiponso anthu a mʼdziko logwirizana naye adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Igupto.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti:
“ ‘Onse othandiza Igupto adzaphedwa
ndipo kunyadira mphamvu zake kudzatheratu.
Adzaphedwa ndi lupanga
kuyambira ku Migidoli mpaka ku mzinda wa Asiwani,’ ”
ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“ ‘Dziko la Igupto lidzasanduka bwinja
kupambana mabwinja ena onse opasuka,
ndipo mizinda yake idzakhala yopasuka
kupambana mizinda ina yonse.
Nditatha kutentha Igupto
ndi kupha onse omuthandiza,
pamenepo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“ ‘Nthawi imeneyo ikadzafika, amithenga adzapita mofulumira kuchokera kwa Ine kukaopseza Kusi, iwowo osadziwako kanthu. Ndipo adzada nkhawa pa tsiku limene Igupto adzawonongedwa, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndidzagwiritsa ntchito Nebukadinezara, mfumu ya ku Babuloni
kuti ndithetse gulu lankhondo la Igupto.
Iye ndi gulu lake lankhondo, mtundu wa anthu ankhanza kwambiri aja
adzabwera kudzawononga dzikolo.
Adzasolola malupanga awo kulimbana ndi Igupto
ndipo dziko lidzadzaza ndi mitembo.
Ndidzawumitsa mtsinje wa Nailo
ndi kugulitsa dziko la Igupto kwa anthu oyipa.
Ndidzagwiritsa ntchito anthu achilendo kuti ndiwononge dzikolo
pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.
Ine Yehova ndayankhula.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Ndidzawononga mafano
ndi kuthetsa milungu yosema ya ku Mefisi.
Simudzakhalanso mfumu mu Igupto,
ndipo ndidzaopseza dziko lonse.
Ndidzasandutsa chipululu mzinda wa Patirosi,
ndi kutentha mzinda wa Zowani.
Ndidzalanga mzinda wa Thebesi.
Ndidzakhuthulira ukali wanga pa mzinda wa Peluziumu,
linga lolimba la Igupto,
ndi kuwononga gulu lankhondo la Thebesi.
Ndidzatentha ndi moto dziko la Igupto;
Peluziumu adzazunzika ndi ululu.
Malinga a Thebesi adzagumuka,
ndipo mzindawo udzasefukira ndi madzi.
Anyamata a ku Oni ndi ku Pibeseti
adzaphedwa ndi lupanga
ndipo okhala mʼmizinda yake adzatengedwa ukapolo.
Ku Tehafinehezi kudzakhala mdima
pamene ndidzathyola goli la Igupto;
motero kunyada kwake kudzatha.
Iye adzaphimbidwa ndi mitambo yakuda,
ndipo okhala mʼmizinda yake adzapita ku ukapolo.
Kotero ndidzalanga dziko la Igupto,
ndipo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Farao Watha Mphamvu
Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi woyamba wa chaka chakhumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Igupto. Taona, silinamangidwe kuti lipole, ngakhale kulilimbitsa ndi nsalu kuti lithe kugwiranso lupanga. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti, Ine ndikudana ndi Farao mfumu ya Igupto. Ndidzathyola manja ake onse; dzanja labwino pamodzi ndi lothyokalo, ndipo lupanga lidzagwa mʼmanja mwake. Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, ndipo mʼmanja mwake ndidzayikamo lupanga langa. Koma ndidzathyola manja a Farao, ndipo adzabuwula ngati wolasidwa koopsa pamaso pa mfumu ya ku Babuloniyo. Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya ku Babuloni, koma manja a Farao adzafowoka. Motero anthu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzayika lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ndipo adzaligwiritsa ntchito pothira nkhondo dziko la Igupto. Ndidzamwaza Aigupto pakati pa mitundu ya anthu, ndikuwabalalitsira ku mayiko ambiri. Motero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Mkungudza mu Lebanoni
Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, unene kwa Farao mfumu ya Igupto ndi gulu lake lankhondo. Awawuze kuti,
“ ‘Kodi mu ukulu wanu ndani angafanane ndi inu?
Taonani, ndidzakufanizirani ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,
wa nthambi zokongola zochititsa mthunzi mʼnkhalango.
Unali wautali,
msonga zake zooneka pamwamba pa nkhalango.
Madzi ndiwo ankawukulitsa mkungudzawo,
akasupe ozama ankawutalikitsa.
Mitsinje yake inkayenda
mozungulira malo amene unaliwo
ndipo ngalande zake zinkafika
ku mitengo yonse ya mʼmunda.
Choncho unatalika kwambiri
kupambana mitengo yonse ya mʼmunda.
Nthambi zake zinachuluka
ndi kutalika kwambiri,
chifukwa inkalandira madzi ambiri.
Mbalame zonse zamlengalenga
zinkamanga zisa zake mʼnthambi za mtengowo.
Nyama zakuthengo zonse
zinkaswanirana mʼmunsi mwa nthambi zake.
Mitundu yotchuka ya anthu
inkakhala mu mthunzi wake.
Unali wokongola kwambiri,
wa nthambi zake zotambalala,
chifukwa mizu yake inazama pansi
kumene kunali madzi ochuluka.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe
mkungudza wofanana nawo,
kapena mitengo ya payini
ya nthambi zofanafana ndi nthambi zake.
Munalibenso mtengo wa mkuyu
nthambi zofanafana ndi zake.
Mʼmunda wa Mulungu munalibe mtengo wina uliwonse
wofanana ndi iwo kukongola kwake.
Ine ndinawupanga wokongola
wa nthambi zochuluka.
Mitengo yonse ya mu Edeni, mʼmunda wa
Mulungu inawuchitira nsanje.
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Chifukwa kuti mtengowo unatalika kwambiri, unatulutsa songa zake mpaka ku thambo, ndipo unadzikweza chifukwa cha msinkhu wake, ndinawupereka mʼdzanja la mfumu ya mitundu ya anthu kuti awulange molingana ndi kuyipa kwake. Anthu ankhanza kwambiri amitundu ya anthu achilendo adzawudula ndi kuwusiya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri ndi mu zigwa zonse. Nthambi zake zidzathyokera mʼmitsinje ya mʼdzikomo. Motero mitundu yonse ya anthu a dziko lapansi amene ankasangalala mu mthunzi wake idzawusiya. Mbalame zonse zamlengalenga zidzakhala pa mtengo wakugwawo, ndipo nyama zakuthengo zonse zidzakhala pa nthambi zake. Zidzakutero kuti pasakhalenso mitengo inanso ya mʼmbali mwa madzi yotalika kwambiri, imene idzatalike kwambiri ndi songa zake kufika mpaka ku mitambo. Komanso kuti pasadzakhalenso mitengo yolandira bwino madzi, imene idzatalika motero. Paja yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita ku dziko lapansi kukhala ndi anthu akufa amene analowa mʼmanda kale.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene mkungudzawo unatsikira ku manda, ndinawuza nyanja kuti iwulire maliro pakuwuphimba. Ndinawumitsa mitsinje ndipo madzi ambiri anaphwa. Ndinabweretsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse ya mʼdzikomo inawuma. Mitundu ya anthu inagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndinawutsitsira ku manda pamodzi ndi iwo amene anafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni pamodzi ndi ya ku Lebanoni yosankhidwa bwino inasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi. Amene ankakhala mu mthunzi wake, amene ankayanjana nawo, iwonso anapita nawo pamodzi ku manda, kukakhala pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu.
“ ‘Ndi mitengo iti ya mu Edeni imene ingafanane ndi kukongola kwako ndi ulemerero wako? Komabe iwenso, udzatsikira ku dziko la anthu akufa pamodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, anthu amene anaphedwa pa nkhondo.
“ ‘Mtengowo ndi Farao ndi gulu lake lankhondo, akutero Ambuye Yehova.’ ”
Nyimbo ya Maliro a Farao
Pa tsiku loyamba la mwezi wa khumi ndi chiwiri, chaka chakhumi ndi chiwiri, Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu imba nyimbo ya maliro a Farao mfumu ya Igupto ndipo uyiwuze kuti,
“Iwe umadziyesa ngati mkango pakati pa mitundu ya anthu.
Koma iwe uli ngati ngʼona mʼnyanja.
Umakhuvula mʼmitsinje yako,
kuvundula madzi ndi mapazi ako
ndi kudetsa madzi mʼmitsinje.
“Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti,
“ ‘Pogwiritsa ntchito gulu la anthu a mitundu yambiri,
ndidzakuponyera khoka langa
ndi kukugwira mu ukonde wanga.
Ndidzakuponya ku mtunda
ndi kukutayira pansi.
Ndidzabweretsa mbalame zamumlengalenga kuti zidzatere pa iwe,
ndipo zirombo zonse za dziko lapansi zidzakudya.
Ndidzayanika mnofu wako pa mapiri
ndipo zigwa zidzadzaza ndi zotsalira zako.
Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi ako,
mpaka kumapiri komwe,
ndipo mitsinje idzadzaza ndi mnofu wako.
Ndikadzakuwononga, ndidzaphimba miyamba
ndikudetsa nyenyezi zake.
Ndidzaphimba dzuwa ndi mtambo,
ndipo mwezi sudzawala.
Zowala zonse zamumlengalenga
ndidzazizimitsa;
ndidzachititsa mdima pa dziko lako,
akutero Ambuye Yehova.
Ndidzasautsa mitima ya anthu a mitundu yambiri
pamene ndidzakupititsa ku ukapolo pakati pa mitundu ya anthu,
ku mayiko amene iwe sunawadziwe.
Ine ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yambiri adabwe nawe,
ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha aakulu chifukwa cha iwe
pamene ndidzaonetsa lupanga langa pamaso pawo.
Pa nthawi ya kugwa kwako,
aliyense wa iwo adzanjenjemera
moyo wake wonse.
“ ‘Pakuti ndikunena Ine Ambuye Yehova kuti,
“ ‘Lupanga la mfumu ya ku Babuloni
lidzabwera kudzalimbana nawe.
Ndidzachititsa gulu lako lankhondo kuti ligwe
ndi lupanga la anthu amphamvu,
anthu ankhanza kwambiri pakati pa mitundu yonse ya anthu.
Adzathetsa kunyada kwa Igupto,
ndipo gulu lake lonse la nkhondo lidzagonjetsedwa.
Ndidzawononga ziweto zake zonse
zokhala mʼmbali mwa madzi ambiri.
Ku madziko sikudzaonekanso phazi la munthu
kapena kudetsedwa ndi phazi la ziweto.
Pambuyo pake ndidzayeretsa madzi ake
ndipo mitsinje yake idzayenda mokometsera ngati mafuta,
akutero Ambuye Yehova.
Ndikadzasandutsa dziko la Igupto kukhala bwinja;
ndikadzawononga dziko lonse
ndi kukantha onse okhala kumeneko,
adzadziwa kuti ndine Yehova.’
“Mawu angawa adzakhala nyimbo ya maliro. Ana a akazi amitundu ya anthu adzayimba, kuyimbira Igupto ndi gulu lake lonse la nkhondo, akutero Ambuye Yehova.”
Pa tsiku la 15 la mwezi woyamba, chaka cha khumi ndi chiwiri, Yehova anayankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu lankhondo la Igupto ndipo uwalowetse pamodzi ndi anthu ena amphamvu a mayiko ena ku dziko la anthu akufa. Ufunse kuti, ‘Ndani amene akukuposa kukongola? Tsikirani ku manda ndi kukhala pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe.’ Aigupto adzagwa pakati pa amene akuphedwa ndi lupanga. Lupanga ndi losololedwa kale. Iye adzaphedwa pamodzi ndi gulu lake lankhondo. Mʼkati mwa manda atsogoleri amphamvu pamodzi ndi ogwirizana nawo azidzakambirana za Igupto nʼkumati, ‘Afika kuno anthu osachita mdulidwe aja! Ndi awa agona apawa, ophedwa pa nkhondo.’
“Asiriya ali komweko ndipo ankhondo ake onse ali mʼmanda omuzungulira. Onsewo anaphedwa pa nkhondo. Manda awo ali kumalo ozama a dzenje, ndipo ankhondo ake azungulira manda ake. Onse amene anaopseza dziko la anthu amoyo aphedwa, agwa ndi lupanga.
“Elamu ali komweko ndipo ankhondo ake ali mʼmanda omuzungulira. Onsewa anaphedwa pa nkhondo, natsikira ku manda ali osachita mdulidwe. Iwowa kale ankaopseza anthu pa dziko lapansi. Tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Amukonzera pogona pakati pa anthu ophedwa, pamodzi ndi gulu lake lonse la nkhondo litazungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe ophedwa ndi lupanga. Paja anthuwa ankaopsa mʼdziko la anthu a moyo. Koma tsopano akuchita manyazi pamodzi ndi amene ali mʼmanda. Iwo ayikidwa pakati pa anthu ophedwa.
“Mesaki ndi Tubala ali komweko, pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo litazungulira manda awo. Onsewo ndi anthu osachita mdulidwe, ophedwa ndi lupanga. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Iwo sanayikidwe mwaulemu ngati ankhondo amphamvu amakedzana, amene anatsikira ku dziko la anthu akufa ndi zida zawo zomwe za nkhondo. Malupanga awo anawayika ku mitu yawo, ndipo zishango zawo anaphimba mafupa awo. Kale anthu amphamvu amenewa ankaopsa dziko la anthu amoyo.
“Iwenso Farao, udzaphwanyidwa ndi kuyikidwa pakati pa anthu osachita mdulidwe, amene anaphedwa ndi lupanga.
“Edomu ali kumeneko pamodzi ndi mafumu ake ndi akalonga ake onse. Ngakhale anali amphamvu, koma anayikidwa. Ayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje.
“Akalonga onse akumpoto pamodzi ndi anthu onse a ku Sidoni ali kumeneko. Anatsikira ku dziko la anthu akufa mwamanyazi ngakhale anali owopsa ndi mphamvu zawo. Iwo akugona osachita mdulidwe pamodzi ndi amene anaphedwa ndi lupanga ndipo akuchita manyazi pamodzi ndi iwo amene anatsikira kale ku manda.
“Farao ndi gulu lake lankhondo akadzawaona iwowa adzathunza mtima pokumbukira kuchuluka kwa gulu lake lankhondo limene linaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Paja ankaopsa mʼdziko la anthu amoyo. Koma Faraoyo pamodzi ndi ankhondo ake onse adzayikidwa pamodzi ndi anthu osachita mdulidwe, pamodzi ndi amene anaphedwa pa nkhondo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Ezekieli Akhala Mlonda
Yehova anandiyankhula nati: “Iwe mwana wa munthu awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Paja zimati ndikatumiza nkhondo mʼdziko anthu a mʼdzikomo amasankha munthu mmodzi pakati pawo kuti akhale mlonda. Tsono iyeyo amati akaona nkhondo ikubwera amaliza lipenga kuti achenjeze anthuwo. Wina aliyense akamva lipenga koma osasamala, mdani uja akabwera nʼkumupha, ndiye kuti wadziphetsa yekha. Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanalabadire. Ndiye kuti wadziphetsa yekha. Akanasamala kuchenjeza kwa mlonda akanapulumuka. Koma ngati mlondayo aona lupanga likubwera ndipo osawomba lipengalo kuchenjeza anthu, ndipo lupanga libwera ndi kuchotsa moyo wa mmodzi mwa iwo, munthu ameneyo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma ndidzamuyimba mlandu mlondayo chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.’
“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuyika kuti ukhale mlonda wa Aisraeli. Choncho imva mawu amene ndikuyankhula ndipo uwachenjeze. Ndikawuza munthu woyipa kuti, ‘Iwe munthu woyipa, udzafa ndithu,’ ndipo iwe osayankhula kumuchenjeza kuti aleke njira zake, munthu wochimwayo adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma Ine ndidzakuyimba mlandu chifukwa cha imfa yake. Koma ngati uchenjeza munthu woyipa kuti aleke njira zake, ndipo iye osatero, adzafa chifukwa cha tchimo lake, koma iwe udzapulumutsa moyo wako.
“Iwe mwana wa munthu, akumbutse Aisraeli mawu awo akuti, ‘Ife talemedwa ndi zolakwa zathu ndi machimo athu, ndipo tikuwonda chifukwa cha zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’ ” Uwawuze kuti, Ine Ambuye Yehova ndikuti: “Pali Ine wamoyo, sindikondwera ndi imfa ya munthu woyipa. Ndimakondwera ndikamaona munthu woyipa akuleka zoyipa zake kuti akhale ndi moyo. Tembenukani! Tembenukani, siyani makhalidwe anu oyipa! Muferanji, Inu Aisraeli?
“Tsono iwe mwana wa munthu, awuze anthu a mtundu wako kuti, ‘Ngati munthu wolungama achimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwino zija sizidzamupulutsa. Koma wochimwa akaleka ntchito zake zoyipazo, sadzalangidwa konse. Ndithu ngati munthu wolungama ayamba kuchimwa sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino zija.’ Ngati ndiwuza munthu wolungama kuti adzafa ndithu, koma iyeyo nʼkumadalira ntchito zake zabwino zimene anachita kale ndi kuyamba kuchimwa, ndiye kuti ntchito zake zabwinozo zidzayiwalika. Iye adzafa chifukwa cha machimo ake. Ndipo ngati ndiwuza munthu woyipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ tsono iye nʼkutembenuka kuleka machimo ake ndi kuyamba kuchita zimene Yehova afuna, monga kubweza chimene anatenga ngati chikole cha ngongole, kubweza chimene anaba, kutsatira malamulo omwe amapereka moyo ndi kuleka kuchita zoyipa, iye adzakhala ndithu ndi moyo; sadzafa. Ndidzakhululuka machimo ake onse anachita. Iye wachita zimene ndi zolungama ndi zoyenera ndipo iye adzakhala ndi moyo ndithu.
“Komabe anthu a mtundu wako akunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, koma makhalidwe awo ndiwo ali osalungama. Ngati munthu wolungama atembenuka ndi kuleka ntchito zake zolungama ndi kuyamba kuchita zoyipa, adzafa nazo. Ndipo ngati munthu woyipa atembenuka ndi kuleka ntchito zake zoyipa ndi kuyamba kuchita zolungama ndi zoyenera, iye adzakhala ndi moyo pochita zimenezo. Koma Inu Aisraeli, mukunena kuti, ‘Zimene Ambuye amachita ndi zopanda chilungamo.’ Ayi, inu Aisraeli, Ine ndidzaweruza aliyense wa inu potsata ntchito zake.”
Mbiri ya Kuwonongeka kwa Yerusalemu
Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka chakhumi ndi chiwiri cha ukapolo wathu, munthu wina amene anapulumuka ku Yerusalemu anabwera kudzandiwuza kuti, “Mzinda wagwa!” Tsono madzulo ake munthuyo asanafike, dzanja la Yehova linali pa ine. Koma mmawa mwake munthuyo atabwera Yehova anatsekula pakamwa panga, motero kuti sindinakhalenso wosayankhula.
Ndipo Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmizinda ya mabwinja ya dziko la Israeli akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo anamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsono dzikolo ndi lathu.’ Choncho iwe uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Inu mumadya nyama ili ndi magazi ake, ndipo mumapembedza mafano ndi kukhetsa magazi, kodi tsono inu nʼkulandira dzikoli? Mumadalira lupanga lanu, mumachita zinthu zonyansa, ndipo aliyense wa inu amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi inu nʼkulandira dzikoli?’
“Uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Ndithu pali Ine wamoyo, anthu amene anatsala mʼmizinda ya mabwinja adzaphedwa ndi lupanga, amene ali ku midzi ndidzawapereka kuti adzadyedwe ndi zirombo zakuthengo, ndipo amene ali mʼmalinga ndi mʼmapanga adzafa ndi mliri. Ndidzalisandutsa chipululu dzikolo, ndipo mphamvu zake zimene amanyadira zidzatheratu, ndipo mapiri a Yerusalemu adzasanduka chipululu, kotero kuti palibe amene adzatha kudutsako. Ndikadzasandutsa dzikolo chipululu chifukwa cha zonyansa zimene ankachita, pamenepo ndiye adzadziwa kuti ndine Yehova.’
“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akumayankhula za iwe akakhala pa makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zawo. Akumawuzana kuti, ‘Tiyeni tikamve uthenga umene wachokera kwa Yehova.’ Anthu anga amabwera kwa iwe, monga momwe amachitira nthawi zonse anthu anga, ndipo amakhala pansi pamaso pako kumvetsera mawu ako. Koma zimene akumvazo sazichita. Zokamba zawo zimaonetsa chikondi, koma mitima yawo imakhala pa phindu lawo. Kunena zoona, kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoyimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poyimba zeze. Kumva amamva mawu ako koma sawagwiritsa ntchito.
“Koma zonsezi zikadzachitika, ndipo zidzachitika ndithu, pamenepo adzadziwa kuti mneneri anali pakati pawo.”
Abusa a Israeli
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, yankhula mawu oyimba mlandu abusa a Israeli. Lengeza ndipo uwawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti, ‘Tsoka kwa abusa a Israeli amene mumangodzisamala nokha! Kodi abusa sayenera kusamalira nkhosa? Mumadya chambiko, mumadziveka zovala zaubweya, ndi kupha nyama zonenepa, koma simusamalira nkhosazo. Simunalimbitse nkhosa zofowoka, kapena kuchiritsa zodwala, kapena kumanga mabala a nkhosa zopweteka. Simunabweze zosochera kapena kufunafuna zotayika. Munaziweta mozunza ndi mwankhanza. Kotero zinabalalika chifukwa zinalibe mʼbusa, ndipo pamene zinabalalika zinakhala chakudya cha zirombo zonse zakuthengo. Nkhosa zanga zinayendayenda mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zazitali. Zinabalalika pa dziko lonse lapansi, ndipo palibe amene anazilondola kapena kuzifunafuna.
“ ‘Choncho Inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. Pali Ine wamoyo, akutero Ambuye Wamphamvuzonse, ndithu, nkhosa zanga zinajiwa ndi zirombo zakuthengo, zinasanduka chakudya cha zirombo chifukwa panalibe abusa. Abusa anga sanafunefune nkhosa zanga. Iwo ankangosamala za iwo okha mʼmalo mosamala nkhosa zanga. Chifukwa chake, inu abusa, tamvani zimene Ine Yehova ndikukuwuzani. Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndayipidwa nanu, inu abusa. Ndidzakulandani nkhosa zanga ndipo simudzazidyetsanso. Ndidzakuchotsani pa ntchito ya ubusa kuti musamangodzidyetsa nokha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga kukamwa kwanu ndipo simudzazidyanso.
“ ‘Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti, mwini wakene ndidzazifunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira. Monga mʼbusa amanka nafunafuna nkhosa zake pamene zina zabalalikira kutali, moteronso Ine ndidzafunafuna nkhosa zanga. Ndidzazipulumutsa kuchoka kumalo onse kumene zinabalalikira pa nthawi yankhungu ndi mdima. Ndidzazitulutsa pakati pa mitundu ya anthu ndi kuzisonkhanitsa kuchokera ku mayiko ena, ndipo ndidzazibwezera ku dziko lawo. Ndidzaziwetera ku mapiri a Israeli, mʼmbali mwa mitsinje ndi kumalo kumene kumakhala anthu. Ndidzaziwetera kumalo a msipu wabwino. Mapiri okwera a Israeli adzakhala malo azidyetserako. Kumeneko zidzapumula ku abusa abwino a msipu ndipo zizidzadyadi msipu wonenepetsa pa mapiri a Israeli. Ine mwini wake ndidzaziweta nkhosa zanga ndi kuzilola kuti zipumule. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndidzafunafuna zotayika ndi kubweza zosochera. Ndidzamanga mabala a zopweteka ndi kulimbikitsa zofowoka. Koma zonenepa ndi zamphamvu ndidzaziwononga. Ndidzaweta nkhosazo mwachilungamo.
“ ‘Kunena za inu, nkhosa zanga, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa, pakati pa nkhosa zazimuna ndi mbuzi zazimuna. Kodi sikukukwanirani kudya msipu wabwino kuti muzichita kuponderezanso msipu umene simunadyewo? Kodi simukhutira ndi kumwa madzi abwino kuti muzinka mudetsanso madzi otsalawo ndi mapazi anu? Kodi nkhosa zanga zidye zimene mwazipondaponda ndi kumwa madzi amene mwawadetsa ndi mapazi anu?
“ ‘Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Taonani, Ine mwini wake ndidzaweruza pakati pa nkhosa zonenepa ndi nkhosa zowonda. Popeza zofowoka mumaziwomba ndi kuzikankhira kumbali, ndipo mumazigunda ndi nyanga zanu nʼkuzimwazira kutali, tsono Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sindidzalolanso kuti zijiwe. Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ina ndi nkhosa inanso. Ndidzaziyikira mʼbusa mmodzi, mtumiki wanga Davide. Iyeyo ndiye azidzazisamala. Adzakhala mʼbusa wawo. Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wake ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu pakati pa nkhosazo. Ine Yehova ndayankhula.
“ ‘Ndidzapangana nazo pangano la mtendere. Ndidzachotsa mʼdzikomo zirombo zolusa. Choncho nkhosa zanga zidzakhala mu mtendere mu chipululu ngakhalenso mʼthengo. Ndidzakhazika anthu anga pafupi ndi phiri langa loyera ndipo ndidzawadalitsa. Ndidzawagwetsera mvula pa nthawi yake ndipo idzakhala mvula ya madalitso. Mitengo ya mʼminda idzabereka zipatso zake, ndipo nthaka idzakhala ndi zokolola zake. Anthu adzakhala mwamtendere mʼdziko lawo. Iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzathyola magoli awo ndi kuwapulumutsa kuchoka mʼmanja mwa amene anawagwira ukapolo. Anthu amitundu ina sadzawafunkhanso ndipo sadzadyedwa ndi zirombo zakuthengo. Adzakhala mwamtendere ndipo palibe amene adzawaopseze. Ndidzawapatsa zokolola zochuluka motero kuti sadzavutikanso ndi njala. Anthu a mitundu ina sadzawanyozanso. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine Yehova Mulungu wawo ndili nawo pamodzi, ndipo kuti iwo, Aisraeli, ndi anthu anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Inu ndinu nkhosa zanga, nkhosa zimene ndimazidyetsa. Ine ndine Mulungu wanu. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse.’ ”
Za Chilango cha Edomu
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, yangʼana phiri la Seiri; yankhula moliyimba mlandu ndipo awawuze anthu a kumeneko kuti zimene ndikuyankhula Ine Ambuye Yehova ndi izi: Inu anthu a ku mapiri a Seiri ndikudana nanu. Ndidzatambasula dzanja langa kulimbana nanu, ndipo ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu. Mizinda yanu ndidzayisandutsa mabwinja, ndipo dziko lanu lidzasanduka chipululu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“Munali adani a Israeli nthawi zonse, ndipo munkalola kuti Aisraeli aphedwe pa nkhondo pa nthawi ya mavuto awo, pa nthawi imene chilango chawo chinafika pachimake. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzakukanthani. Imfa idzakulondolani. Popeza sunadane nako kukhetsa magazi, imfa idzakulondola. Phiri la Seiri ndidzalisandutsa chipululu ndipo ndidzapha onse amene amapita nabwerera kumeneko. Ndidzaza mapiri ake ndi mitembo. Ophedwa pa nkhondo adzagwera pa zitunda zanu, zigwa zanu ndi mʼmitsinje yanu yonse. Ndidzasandutsa dziko lanu kukhala chipululu mpaka muyaya, ndipo mʼmizinda yanu simudzakhalanso anthu. Zikadzachitika izi mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.
“Inu munanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu, Yuda ndi Israeli, pamodzi ndi mayiko awo omwe idzakhala yathu.’ Munanena chomwechi ngakhale kuti Ine Yehova ndinali momwemo. Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pali Ine wamoyo, ndithu ndidzachita nanu monga munachita ndi anthu a ku Yuda ndi Israeli poonetsa mkwiyo wanu, nsanje yanu ndi chidani chanu pa iwo. Ndikadzakulangani mudzandidziwadi pakati panupo. Ndipo mudzadziwa kuti Ine Yehova ndinamva mawu anu onse onyoza amene munanena molimbana ndi mapiri a Israeli. Inu munati, ‘Mapiri a Israeli asanduka bwinja, ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwawononge.’ Mawu anu amene munayankhula monyada kundinyoza Ine ndinawamva. Ine Ambuye Yehova ndikuti: Dziko lonse lapansi lidzasangalala pamene ndidzakusandutsani bwinja. Monga momwe inu munasangalala pamene anthu anga Aisraeli anagwa, Inenso ndidzakuchitani chimodzimodzi. Udzasanduka bwinja, iwe Phiri la Seiri, iwe ndi dziko lonse la Edomu. Zikadzatero anthu onse adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Kubwezeretsedwa kwa Israeli
“Iwe mwana wa munthu, yankhula kwa mapiri a Israeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a Israeli, imvani mawu a Yehova.’ Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mdani wanu ankanena kuti, ‘Aa! Dziko lamapiri lakalekale lija lasanduka lathu.’ Choncho nenera ndipo uwawuze kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anakusakazani ndi kukuponderezani ku mbali zonse motero kuti munakhala mʼmanja mwa anthu a mitundu ina yonse ndipo anthu ankakunenani ndi kukunyozani, choncho, inu mapiri a Israeli, imvani zimene Ine Ambuye Yehova ndikuwuza mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa, mabwinja ndi mizinda yosiyidwa imene yakhala ikufunkhidwa komanso kunyozedwa ndi anthu a mitundu ina okuzungulirani. Tsono Ine Ambuye Yehova ndikuti: Mu mkwiyo wanga woopsa ndinayankhula kuyimba mlandu mitundu ina yonse ya anthu makamaka a ku Edomu. Iwowa mwa chimwemwe chodzaza tsaya ndi mwa nkhwidzi analanda dziko langa ndi kulisandutsa lawo ndi kutengeratu dziko la msipu kukhala lawo.’ Nʼchifukwa chake, lengeza ku dziko la Israeli, ndipo uwuze mapiri ndi magomo, zigwembe ndi zigwa kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndikuyankhula ndi mtima wokwiya kwambiri chifukwa inu munalandira chitonzo cha anthu a mitundu ina.’ Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu ya anthu idzatozedwanso.
“Koma Inu mapiri a Israeli mudzaphukanso nthambi ndipo mudzawabalira zipatso anthu anga a Israeli, pakuti ali pafupi kubwerera kwawo. Taonani, Ine ndili mbali yanu ndipo ndidzakukomerani mtima. Mudzalimidwa ndi kudzalidwa. Ndidzachulukitsa chiwerengero cha anthu anu, nyumba yonse ya Israeli. Mʼmizinda mudzakhalanso anthu ndipo mabwinja adzamangidwanso. Ndidzachulukitsa chiwerengero cha amuna pamodzi ndi ziweto zomwe, ndipo adzachuluka kwambiri ndi kubereka ana ambiri. Ndidzakhazika anthu mʼdzikomo monga analili kale, ndi kukulemeretsani kuposa kale. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova. Ndidzachititsa anthu kuyenda pa inu, ndiye kuti inu anthu anga Aisraeli. Iwowo adzakhazikika pa inu, ndipo inu mudzakhala cholowa chawo. Simudzalandanso ana awo.
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Popeza anthu amanena kuti, ndiwe dziko limene limadya anthu ake ‘kulanda ana a mtundu wake,’ nʼchifukwa chake, simudzadyanso anthu kapena kulanda ana a mtundu wako. Ine Ambuye Yehova ndikutero. Sindidzakulolaninso kumva mnyozo wa anthu a mitundu ina, kapena kupirira kunyogodola kwawo kapenanso kupunthwitsanso anthu a mʼdziko lako. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Yehova anandiyankhulanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, pamene anthu a Israeli ankakhala mʼdziko lawolawo, analiyipitsa ndi makhalidwe awo ndiponso zochita zawo. Machitidwe awo pamaso panga anali onyansa pa zachipembedzo ngati msambo wa mkazi amene ali pa nthawi yake. Tsono ndinawalanga chifukwa cha magazi amene anakhetsa mʼdzikomo, ndiponso chifukwa anayipitsa dziko ndi mafano awo. Ndinawamwaza pakati pa anthu a mitundu ina ndipo anabalalikira mʼmayiko onse. Ndinawalanga molingana ndi makhalidwe awo ndi zochita zawo. Atafika kwa anthu a mitundu ina, kulikonse kumene anapitako, anayipitsa dzina langa loyera. Zinatero popeza anthu ponena za iwo ankanena kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, komatu anachotsedwa ku dziko lake.’ Koma Ine ndinkadera nkhawa dzina langa loyera, limene Aisraeli analiyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapitako.
“Nʼchifukwa chake awuze Aisraeliwo kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ine ndidzachita zimene ndidzachitezo osati chifukwa cha inuyo Aisraelinu ayi, koma chifukwa cha dzina langa, limene mwaliyipitsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapitako. Ndidzaonetsa chiyero cha dzina langa lotchuka, limene layipitsidwa pakati pawo. Anthu a mitundu inayo atadzazindikira kuti ndaonetsa kudzera mwa inu kuti dzina langa ndi loyera, iwo adzadziwanso kuti Ine ndine Yehova. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“Pakuti Ine ndidzakuchotsani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzakusonkhanitsani kuchoka ku mayiko onse ndi kukubwezerani ku dziko lanulanu. Ndidzakuwazani madzi oyera, ndipo mudzakhala oyera mtima. Zonse zimene zimakuyipitsani zidzachoka. Ndidzakuyeretsani pochotsa mafano anu onse. Ndidzakupatsani mtima watsopano ndi kulowetsa mzimu watsopano mwa inu. Ndidzachotsa mwa inu mtima wanu wowuma ngati mwala ndi kukupatsani mtima wofewa ngati mnofu. Ndipo ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzakuthandizani kutsatira malangizo anga ndi kukusungitsani mosamala kwambiri malamulo anga. Mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Ndidzakupulumutsani ku zonse zokuyipitsani. Ndidzakuchulukitsirani tirigu ndipo sindidzakugwetseraninso njala. Ndidzachulukitsa zipatso za mʼmitengo yanu ndi zokolola za mʼmunda mwanu, kotero kuti simudzanyozedwanso pakati pa anthu a mitundu ina chifukwa cha njala. Pamenepo mudzakumbukira makhalidwe anu oyipa ndi ntchito zanu zoyipa. Machimo anu ndi ntchito zanu zonyansa zidzakuchititsa nokha manyazi. Tsono dziwani kuti Ine sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo ayi, ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Ndiyetu chitani manyazi ndipo mugwetse nkhope zanu, inu Aisraeli chifukwa cha makhalidwe anu!
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limene ndidzayeretse machimo anu onse, ndidzayikamonso anthu mʼmizinda yanu, ndipo ndidzamanganso nyumba pa mabwinja. Dziko limene linasanduka chipululu lizidzalimidwanso. Mʼmalo moti aliyense wopitamo alione dzikolo ngati chipululu tsopano adzaliona lolimidwa. Iwo adzati, ‘Dziko ili, limene linali chipululu, lasanduka munda wa Edeni. Mizinda imene inali mabwinja osiyidwa ndi owonongedwa, tsopano ndi yotetezedwa ndi yokhalamo anthu. Ndipo anthu a mitundu ina okhala pafupi nanu amene anatsala adzadziwa kuti Ine Yehova ndine amene ndinamanganso mizinda yowonongeka ndi kudzalanso zinthu zatsopano mʼmalo mʼmene munali chipululu. Ine Yehova ndayankhula ndipo ndidzazichitadi.’
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzalolanso Aisraeli kuti andipemphe zoti ndiwachitire: Ndidzachulukitsa anthu awo ngati nkhosa. Adzachulukadi ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu pa nthawi za chikondwerero. Choncho mizinda ya mabwinja idzadzaza ndi anthu. Zikadzatero adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Chigwa cha Mafupa Owuma
Dzanja la Yehova linali pa ine, ndipo Mzimu wa Yehova unandinyamula nʼkukandikhazika pakati pa chigwa. Chigwacho chinali chodzaza ndi mafupa. Yehova anandiyendetsa uku ndi uku pakati pa mafupawo. Mafupawo anali ochuluka kwambiri mʼchigwa monsemo ndipo anali owuma kwambiri. Tsono Yehova anandifunsa kuti, “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupa amenewa angakhalenso ndi moyo?”
Ndinayankha kuti, “Inu Ambuye Yehova, Inuyo nokha ndiye mukudziwa.”
Pamenepo anandiwuza kuti, “Lengeza kwa mafupa amenewa ndi kuwawuza kuti amve mawu a Ine Yehova! Uwawuze kuti zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kwa mafupa ndi izi: Ndidzawuzira mpweya mwa inu, ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Ndidzakupatsani mitsempha ndi mnofu. Ndiponso ndidzakukutani ndi khungu. Pambuyo pake ndidzawuzira mpweya mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pamenepo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”
Ndipo ndinanenera monga anandilamulira. Ndipo pamene ndinkanenera, ndinamva gobedegobede, ndipo mafupa aja anayamba kulumikizana, fupa ku fupa linzake. Ine ndinayangʼana, ndipo mitsempha ndi mnofu zinabwera pa mafupawo ndipo khungu linaphimba pamwamba pake, koma munalibe mpweya mwa iwo.
Tsono Yehova anandiwuza kuti, “Nenera kwa mpweya, nenera iwe mwana wa munthu ndi kuwuza mpweya mawu a Ine Ambuye Yehova kuti, ‘Bwera kuno iwe mpweya. Bwera kuchokera ku mbali zonse zinayi ndi kudzawuzira anthu ophedwawa kuti akhalenso ndi moyo.’ Choncho ndinanenera monga anandilamulira ndipo mpweya unalowa mwa iwo; apo anthu akufawo anakhala ndi moyo, nayimirira ndipo linali gulu lalikulu lankhondo.”
Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, mafupa awa ndi nyumba yonse ya Israeli. Iwo amanena kuti, ‘Mafupa athu awuma ndipo chiyembekezo chathu chatayika, ife tawonongeka!’ Nʼchifukwa chake nenera ndi kuwawuza kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu anthu anga, ndidzafukula manda anu, ndipo ndidzakutulutsanimo ndi kukubwezerani ku dziko la Israeli. Ndipo inu, anthu anga, mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova, pamene ndidzafukula manda anu ndikukutulutsanimo. Ine ndidzayika Mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhalanso ndi moyo. Pambuyo pake ndidzakulowetsani mʼdziko lanulanu. Choncho mudzadziwa kuti Ambuye Yehova ndayankhula zimenezi, ndipo ndidzazichitadi. Ndikutero Ine Yehova!’ ”
Dziko Limodzi Kutsogoleredwa ndi Mfumu Imodzi
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tenga ndodo ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisraeli oyanjana nawo.’ Utengenso ndodo ina ndipo ulembepo kuti, ‘Ndodo ya Efereimu, ndiye kuti fuko la Yosefe ndi Aisraeli onse oyanjana nawo.’ Ulumikize ndodo ziwirizi kuti zikhale ndodo imodzi mʼdzanja lako.
“Anthu a mtundu wako akadzakufunsa tanthauzo la zimenezi iwe udzawawuze mawu awa a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndidzatenga ndodo ya Yosefe imene ili mʼdzanja la Efereimu, ndi ya mafuko a Aisraeli oyanjana naye, ndi kuyilumikiza ku ndodo ya Yuda, kuti zikhale ndodo imodzi, ndipo zidzakhaladi ndodo imodzi mʼdzanja langa!’ Ndodo ziwiri zimene udzalembepozo zikadzakhala mʼmanja mwako pamaso pa anthu onse, udzawawuze kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ndidzawachotsa Aisraeli pakati pa anthu a mitundu ina kumene anapita ku ukapolo. Ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mbali zonse ndi kubwera nawo ku dziko lawolawo. Ndidzawasandutsa mtundu umodzi mʼdzikomo, pa mapiri a Israeli. Padzakhala mfumu imodzi yowalamulira, ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawikana maufumu awiri. Sadzadziyipitsanso ndi mafano awo, kapena ndi zinthu zawo zonyansa, kapenanso ndi ntchito zawo zoyipa zilizonse. Ndidzawapulumutsa ku machimo awo onse ndi kuwayeretsa. Choncho adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo.
“ ‘Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo, motero onsewa adzakhala ndi mʼbusa mmodzi. Iwo adzatsatira malamulo anga ndipo adzasamalira kusunga malangizo anga. Iwo adzakhala mʼdziko limene ndinalipereka kwa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhalamo. Iwo ndi ana awo pamodzi ndi zidzukulu zawo adzakhala kumeneko ndipo Davide adzakhala mfumu yawo kwa muyaya. Ndidzachita nawo pangano lamtendere; lidzakhala pangano lamuyaya. Ndidzawakhazikitsa ndi kuwachulukitsa, ndipo ndidzayika malo anga opatulika pakati pawo kwamuyaya. Nyumba yanga yokhalamo idzakhala pakati pawo; Ine ndidzakhala Mulungu wawo, ndipo iwo adzakhala anthu anga. Pamenepo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti Ine Yehova ndiye amene ndimasandutsa Israeli kukhala woyera, pamene malo anga opatulika adzakhala pakati pawo kwamuyaya!’ ”
Za Chilango cha Gogi
Yehova anandiyankhula kuti: “Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa Gogi, wa ku dziko la Magogi, amene ali kalonga wamkulu wa mzinda wa Mesaki ndi Tubala. Umuyimbe mlandu. Umuwuze mawu a Ine Ambuye Yehova akuti, ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa ku Mesaki ndi Tubala. Ndidzakuzunguza, ndidzakukola ndi mbedza mʼkamwa mwako. Ndidzakutulutsa iweyo pamodzi ndi gulu lako lonse la nkhondo, akavalo ako ndi okwerapo ake. Onse adzakhala atanyamula zida za nkhondo, zishango ndi malihawo ndipo malupanga awo adzakhala osolola. Pamodzi ndi iwowo, padzakhalanso ankhondo a ku Perisiya, ku Kusi, ndi ku Puti. Onsewa adzakhala atanyamula zishango ndi kuvala zipewa zankhondo. Padzakhalanso Gomeri pamodzi ndi ankhondo ake onse ndiponso banja la Togarima ndi gulu lake lonse lankhondo lochokera kutali kumpoto. Padzakhaladi mitundu yambiri ya anthu pamodzi ndi iwe.
“ ‘Konzekani! Mukhaledi okonzeka, iweyo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo limene lakusonkhanira. Iweyo udzawatsogolera pokamenya nkhondo. Pakapita masiku ambiri ndidzakuyitana. Zaka zikubwerazi ndidzakulowetsa mʼdziko limene lapulumuka ku nkhondo. Anthu ake anasonkhanitsidwa kuchokera ku mitundu ya anthu ambiri nʼkukakhazikika pa mapiri a Israeli amene kwa nthawi yayitali anali ngati chipululu. Anthu onsewa tsopano akukhala mwa mtendere. Tsono iwe pamodzi ndi ankhondo ako onse ndiponso mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe mudzabwera ngati mphepo yamkuntho. Mudzaphimba dziko lonse ngati mitambo.
“Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku limenelo mu mtima mwako mudzabwera maganizo ofuna kukonzekera kuchita zoyipa. Iwe udzanena kuti, ‘Ndikukathira nkhondo dziko la midzi yopanda mipanda; ndikathira nkhondo anthu okhala mwamtendere, anthu amene satchinjirizidwa ndi mipanda, zipata kapena mipiringidzo. Ndipita kukalanda chuma chawo ndi kukafunkha zinthu zawo. Ndidzalimbana ndi midzi imene kale inali mabwinja. Ndikathira nkhondo anthu amene anasonkhanitsidwa kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Iwowa ali ndi ziweto zambiri, katundu wochuluka ndiponso amakhala pakatikati pa dziko lapansi.’ Anthu a ku Seba, a ku Dedani ndiponso amalonda a ku Tarisisi pamodzi ndi midzi yake yonse adzakufunsa kuti, ‘Kodi wabwera kudzafunkha? Kodi wasonkhanitsa gulu lako la nkhondo kudzalanda chuma, kudzatenga siliva ndi golide, ziweto ndi katundu kuti zikhale zofunkha zochuluka?’ ”
“Nʼchifukwa chake, iwe mwana wa munthu, nenera ndipo uwuze Gogi kuti, ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa nthawi imene anthu anga adzakhala pa mtendere, iwe udzanyamuka. Udzabwera kuchokera ku dziko lako kutali kumpoto, iwe pamodzi ndi mitundu yambiri ya anthu imene ili nawe, onse okwera akavalo, gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu. Udzabwera kudzalimbana ndi anthu anga Aisraeli ngati mtambo wophimba dziko. Masiku amenewo, iwe Gogi, ndidzabwera nawe kuti ulimbane ndi dziko langa, kuti anthu a mitundu ina andidziwe Ine, pamene ndidzaonetsa kuyera kwanga pa zimene ndidzakuchite iweyo.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Kodi iwe si amene ndinayankhula za iwe masiku amakedzana kudzera mwa atumiki anga aneneri a Israeli? Pa zaka zambiri iwo ankalengeza kuti ndidzawutsa iwe kuti udzalimbane ndi Israeli. Zimene chidzachitika pa tsiku limenelo ndi izi: Gogi akadzathira nkhondo dziko la Israeli, mkwiyo wanga woopsa udzayaka. Ndikutero Ine Ambuye Wamphamvuzonse. Chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanga woyakawo Ine ndikunenetsa kuti pa nthawi imeneyo padzakhala chivomerezi chachikulu mʼdziko la Israeli. Nsomba za mʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zirombo zakuthengo, cholengedwa chilichonse chimene chimakwawa pansi, ndiponso anthu onse okhala pa dziko lapansi, adzanjenjemera pamaso panga. Mapiri adzangʼambika, malo okwera kwambiri adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwa pansi. Ndidzawutsira Gogi nkhondo kuchokera ku mapiri anga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu a Gogiyo adzaphana okhaokha ndi malupanga. Ine ndidzamulanga ndi mliri ndi imfa. Ndidzagwetsa mvula yoopsa ya matalala, ndiponso sulufule ndi miyala ya moto pa iye ndi pa asilikali ake ndiponso pa mitundu yambiri ya anthu imene ili naye. Motero ndidzadzionetsa kuti ndine wamphamvu ndi woyera. Ndiponso ndidzadziwika pamaso pa anthu a mitundu ina yambiri. Momwemo adzadziwadi kuti Ine ndine Yehova.’ ”
“Iwe mwana wa munthu, nenera modzudzula Gogi ndi kumuwuza kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: ‘Ine ndikudana nawe, iwe Gogi, kalonga wamkulu wa Mesaki ndi Tubala. Ine ndidzakuzunguza ndi kukupirikitsira kutsogolo. Ndidzakutenga kuchokera kutali kumpoto ndi kukutumiza kuti ukalimbane ndi anthu a ku mapiri a Israeli. Kenaka Ine ndidzathyola uta wa mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzagwetsa mivi ya mʼdzanja lako lamanja. Udzagwa ku mapiri a ku Israeli, iwe ndi magulu ako onse ankhondo ndiponso mitundu ya anthu imene ili nawe. Ndidzakusandutsa chakudya cha mitundu yonse ya mbalame zodya nyama, ndiponso cha zirombo zakuthengo. Udzafera pa mtetete kuthengo, pakuti Ine ndayankhula. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndidzatumiza moto pa Magogi ndi pa onse amene amakhala mwamtendere mʼmbali mwa nyanja. Choncho adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’
“Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Israeli. Sindidzalola kuti dzina langa liyipitsidwenso, ndipo mitundu ya anthu idzadziwa kuti Ine Yehova ndine Woyera mu Israeli. Zikubwera! Ndipo zidzachitikadi, ndikutero Ine Ambuye Yehova. Ndiye tsiku limene ndinanena lija.
“Pamenepo okhala mʼmizinda ya Israeli adzatuluka ndipo adzasonkhanitsa zida zankhondo kuti zikhale nkhuni ndipo adzazitentha; zishango ndi lihawo, mauta ndi mivi, zibonga za nkhondo ndi mikondo. Adzazisonkhera moto kwa zaka zisanu ndi ziwiri. Iwo sadzatolera nkhuni kuthengo kapena kukadula ku nkhalango, chifukwa adzasonkhera moto zidazo. Ndipo iwo adzafunkha amene anawafunkhawo, ndi kulanda chuma cha amene anawalanda, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“Pa tsiku limenelo ndidzamupatsa Gogi manda mu Israeli, mʼchigwa cha apaulendo, kummawa kwa Nyanja Yakufa. Mandawo adzatseka njira ya apaulendo, chifukwa Gogi ndi gulu lake lankhondo adzayikidwa kumeneko. Ndipo chigwacho chidzatchedwa chigwa cha gulu lankhondo la Gogi.
“Nyumba ya Israeli idzakhala ikukwirira mitembo kwa miyezi isanu ndi iwiri ndi cholinga choyeretsa dziko. Anthu onse a mʼdzikomo adzakwirira nawo mitembo. Ntchito imeneyo adzatchuka nayo pa tsiku limene ndidzaonetsa ulemerero wanga. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“Patapita miyezi isanu ndi iwiri adzalemba ntchito anthu ena odzayenda mʼdziko lonse kufunafuna mitembo imene inatsalira nʼkumayikwirira. Choncho adzayeretseratu dzikolo. Poyenda mʼdzikomo azidzati akaona fupa la munthu azidzayikapo chizindikiro pambali pake mpaka okumba manda atakalikwirira fupalo ku chigwa cha gulu lankhondo la Gogi. (Komwekonso kudzakhala mzinda wotchedwa Gulu la nkhondo). Ndipo potero adzayeretsa dziko.
“Tsono iwe mwana wa munthu, Ine Ambuye Yehova ndikuti: Itana mbalame za mitundu yonse ndi zirombo zonse zakuthengo ndipo uziwuze kuti, ‘Sonkhanani ndipo bwerani kuchokera ku mbali zonse ku nsembe imene ndikukonzerani inu, nsembe yayikulu pa mapiri a Israeli. Kumeneko inu mudzadya mnofu ndi kumwa magazi. Mudzadya mnofu wa anthu ankhondo amphamvu ndi kumwa magazi a akalonga a dziko lapansi. Onsewo anaphedwa ngati nkhosa zazimuna, ana ankhosa onenepa, mbuzi ndiponso ngati ngʼombe zazimuna zonenepa za ku Basani. Ku phwando lansembe limene ndikukonzera inulo, mudzadya zonona mpaka kukhuta ndi kumwa magazi mpaka kuledzera. Pa tebulo langa mudzakhuta pakudya akavalo ndi okwerapo ake, anthu amphamvu ndi asilikali amitundumitundu,’ ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“Ine ndidzaonetsa ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina, ndipo adzaona mmene ndidzawalangire ndikadzayika dzanja langa pa iwo. Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo Aisraeli adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo. Ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti anthu a Israeli anatengedwa ukapolo chifukwa cha tchimo lawo, chifukwa anali osakhulupirika kwa Ine. Choncho Ine ndinawabisira nkhope yanga ndi kuwapereka kwa adani awo. Motero anaphedwa pa nkhondo. Ndinawachita zimenezi chifukwa cha kunyansa kwawo ndi zolakwa zawo, ndipo ndinawabisira nkhope yanga.
“Nʼchifukwa chake Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsopano ndidzakhazikanso pa bwino banja la Yakobo. Ndidzachitira chifundo Aisraeli onse, ndipo ndidzateteza dzina langa loyera. Anthuwo akadzakhala mwamtendere mʼdziko lawo popanda wina wowaopseza, pamenepo adzayiwala zamanyazi zawo zimene zinawachitikira chifukwa chosandikhulupirira Ine. Ndidzawabwezeranso kwawo kuchokera pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawasonkhanitsa kuchokera ku mayiko a adani awo. Poteropo ndidzaonetsa pamaso pa anthu a mitundu yambiri kuti ndine Woyera. Pamenepo iwo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wawo, ngakhale kuti ndinawapereka ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina. Ine ndidzawasonkhanitsanso ku dziko lawo osasiyako wina mʼmbuyo. Ine sindidzawabisiranso nkhope yanga, pakuti ndidzathira Mzimu wanga pa Aisraeli. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Malo Atsopano a Nyumba ya Mulungu
Kumayambiriro a chaka cha 25, cha ukapolo wathu, tsiku la khumi lamwezi, patapita zaka khumi ndi zinayi mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, pa tsiku lomwelo dzanja la Yehova linali pa ine ndipo Iye anapita nane ku Yerusalemu. Mʼmasomphenyawo Yehova ananditenga ndi kupita nane ku dziko la Israeli ndipo anandiyika pa phiri lalitali kwambiri, moti ndinaona ngati mzinda. Atandifikitsa kumeneko ndinaona munthu wonyezimira ngati mkuwa. Iye anali atayima pa chipata ndipo mʼdzanja lake munali chingwe cha nsalu yabafuta ndi ndodo yoyezera. Munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, penyetsetsa ndipo umvetse bwinobwino. Uyikepo mtima wako pa zonse zimene ndikukuonetsa pakuti anakubweretsa kuno kuti uwone zimenezi. Tsono ukawawuze Aisraeli zonse zimene uzione.”
Chipata Chakummawa
Ine ndinaona khoma litazungulira mbali zonse za Nyumba ya Mulungu. Mʼdzanja la munthuyo munali bango lopimira limene kutalika kwake kunali kwa mamita atatu. Atayeza chipupacho anapeza kuti kuchindikira kwake kunali mamita atatu, ndiponso kutalika kwake kunalinso mamita atatu.
Anapita ku chipata chakummawa. Anakwera pa makwerero a nyumbayo, nayeza chiwundo choyamba cha chipatacho; kutalika kwake kunali mamita atatu. Kudutsa chiwundo choyambachi, panali zipinda za alonda zisanu ndi chimodzi, zitatu kudzanja lamanja, zitatu kudzanja lamanzere. Chilichonse chinali cha mamita atatu mulitali mwake, chimodzimodzinso mulifupi mwake. Mipata ya pakati pa zipindazo inali ya mamita awiri ndi theka. Ndipo chiwundo cha pa chipata pafupi ndi khonde lapachipata, chinali mamita atatu.
Ndipo iye anayeza khonde la chipata ndipo chinali cha mamita atatu. Anayeza khonde ndipo linali mamita anayi. Mphuthu zake zinali mita imodzi kuchindikira kwake. Khonde lamʼkati lapachipata linali kumapeto kwenikweni pafupi ndi Nyumba ya Mulungu.
Mʼkati mwa chipata chakummawa munali zipinda za alonda zitatu mbali iliyonse. Zitatu zonsezo zinali zofanana, ndipo khonde la pakati pa zipindazo linali lofanana. Kenaka anayeza chipata cholowera; mulifupi mwake munali mamita asanu ndipo mulitali mwake munali mamita asanu ndi limodzi ndi theka. Kutsogolo kwa chipinda chilichonse cha alonda kunali khoma lalifupi lotalika theka la mita, ndipo mbali iliyonse ya zipinda za alondazo inali yotalika mamita atatu. Ndipo anayeza kutalika kwa mulifupi mwa chipata cholowera, kuchokera ku khoma lakumbuyo la chipinda chimodzi mpaka ku khoma la chipinda china; kuchokera ku chitseko mpaka ku chitseko china. Kutalika kwake kunali mamita khumi ndi awiri ndi theka. Anayezanso khonde lamʼkati ndipo linali la mamita makumi atatu. Ndipo mozungulira khondelo munali bwalo. Muyesowu sukuphatikiza khonde loyangʼanana ndi bwalo. Kuchokera pa chipata cholowera mpaka ku mapeto a khonde la chipata, kutalika kwake kunali mamita 27. Makoma a zipinda ndiponso makoma a pakati pa zipindazo anali ndi mazenera. Khonde lamʼkati linalinso ndi mazenera mʼkati mwake. Pa makoma onsewo anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Bwalo la Kunja
Kenaka munthuyo anandilowetsa mʼbwalo lakunja, ndipo ndinaona zipinda zina ndi msewu wa miyala wozungulira bwalo lonse. Zipinda zonse zinali makumi atatu ndipo zinkayangʼana msewuwo. Utali wa mulifupi mwa msewuwo unkayenda mamita 27 kufanana ndi utali wa chipata cholowera. Uwu unali msewu wa mʼmunsi. Tsono, anayeza kutalika kwa bwalo kuyambira chipata cholowera choyamba mpaka polowera pa chipata chakunja cha bwalo la mʼkati. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipata Chakumpoto
Kenaka munthuyo anayeza mulitali ndi mulifupi mwa chipata chimene chimayangʼana kumpoto, chotulukira kunja. Zipinda za alonda zimene zinalipo zitatu mbali iliyonse, makoma ake ndi khonde zinali ndi muyeso wofanana ndi wachipata choyamba chija. Kutalika kwake kunali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. Mipata yake, khonde lake ndi zojambula za kanjedza zinali ndi miyeso yofanana ndi za chipata chakummawa. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndipo kotsirizira kwa chipatacho kunali khonde. Panalinso chipata cholowera ku bwalo lamʼkati chofanana ndi chakummawa chimene chimayangʼanana ndi chipata chakumpoto, chofanana ndi cha mbali ya kummawa. Anachiyeza kuchokera ku chipata china mpaka ku chipata china. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipata Chakummwera
Ndipo munthuyo anapita nane ku mbali yakummwera ndipo ndinaona chipata chakummwera. Iye anayeza mphuthu zake ndi khonde ndipo zinali ndi miyeso yofanana ndi ya zina zija. Mʼzipinda za chipata cholowera chimenechi ndi mʼkhonde lake munali mipata yofanana ndi ya mʼzipinda zina. Mulitali mwake munali mamita 27, mulifupi mwake munali mamita 13. Chipatacho chinali ndi makwerero asanu ndi awiri ndi khonde kotsirizira kwake. Chipindacho chinali ndi zojambula za kanjedza ku mbali zonse za makoma. Bwalo lamʼkati linalinso ndi chipata kummwera. Munthuyo analiyeza kuchokera ku chipata chimenechi mpaka ku chipata chakunja. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Zipata Zolowera ku Bwalo la Mʼkati
Ndipo munthu uja anandilowetsa mʼbwalo lamʼkati kudzera ku chipata chakummwera. Anayeza chipatachi ndipo chinali chofanana ndi zinzake zija. Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake zinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi munali mamita 13. (Khonde lililonse la makonde atatu a zipata zolowera bwalo lamʼkati aja linali la mamita ozungulira mʼbwalo lamʼkati anali mamita 13 mulitali mwake, mamita awiri ndi theka mulifupi mwake). Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Kenaka munthuyo anapita nane ku bwalo la mʼkati mbali ya kummawa, ndipo anayeza chipata cholowera; chinali chofanana ndi zinzake zina zija. Zipinda zake za alonda, makoma ake ndi khonde lake zinali zofanana ndi zina zija. Chipata cholowera ndi khonde lake chinali ndi mipata mʼmbali zonse. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. Khonde lake linayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu pake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Kenaka anapita nane ku chipata chakumpoto ndipo anachiyeza. Chinali chofanana ndi zina zija. Zipinda zake za alonda, makoma ake ndiponso khonde lake zinali zofanana ndi zina zija, ndipo chinalinso ndi mipata mbali zonse ziwiri. Mulitali mwake munali mamita 27 ndipo mulifupi mwake munali mamita 13. Khonde lake limayangʼanana ndi bwalo lakunja. Pa mphuthu zake anajambulapo zithunzi za kanjedza mbali zonse ziwiri, ndipo linali ndi makwerero asanu ndi atatu.
Zipinda Zokonzeramo Nsembe
Panali chipinda ndipo khomo lake linali pafupi ndi khonde la chipata cholowera chamʼkati. Mʼchipinda mʼmenemo ankatsukira nyama ya nsembe yopsereza. Pa khonde la chipatacho panali matebulo awiri, lina kuno lina uko. Ankapherapo nsembe zopsereza, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula. Panali matebulo anayi, awiri a iwo anali kunja kwa khoma la khonde pafupi ndi makwerero olowera pa chipata chakumpoto ndi awiri enawo anali mbali inayo ya makwerero. Choncho ku mbali imodzi ya chipata kunali matebulo anayi, ndiponso ku mbali inayo kunali matebulo anayi. Onse pamodzi anali matebulo asanu ndi atatu. Pa matebulopo ankapherapo nyama za nsembe zopsereza. Matebulo anayiwa anali a miyala yosema. Lililonse mulitali mwake linali la masentimita 75, mulifupi mwake linali la masentimita 75, ndipo msinkhu wake unali wa masentimita makumi asanu. Pa matebulopo amayikapo zipangizo zophera nsembe zopsereza ndi nsembe zina. Choncho pa matebulopo ankayikapo nyama za nsembe zopsereza. Mbedza zitatu zazitali ngati chikhatho amazikoleka pa makoma pozungulira ponse.
Zipinda za Ansembe
Munthu uja anapita nane mʼkati mwa bwalo ndipo ndinaona zipinda ziwiri. Chimodzi chinali pafupi ndi chipata chakumpoto kuyangʼana kummwera ndi china chinali pafupi ndi chipata chakummwera kuyangʼana kumpoto. Munthuyo anandiwuza kuti, “Chipinda chimene chikuyangʼana kummwera ndi cha ansembe amene amayangʼanira Nyumba ya Mulungu, ndipo chipinda chimene chikuyangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amayangʼanira guwa lansembe. Amenewa ndiwo ana a Zadoki, ndipo ndi okhawo mwa zidzukulu za Levi amene ayenera kutumikira pamaso pa Yehova mʼNyumba ya Mulungu.”
Kenaka munthuyo anayeza bwalo; linali lofanana mbali zonse kutalika kwake, mulitali mwake munali mamita 53, ndipo mulifupi mwake munali mamita 53. Ndipo guwa lansembe linali kutsogolo kwa Nyumba ya Mulungu.
Nyumba ya Mulungu
Munthuyo anapita nane pa khonde la Nyumba ya Mulunguyo. Anayeza mphuthu za khondelo ndipo zinali mamita awiri ndi theka mbali zonse. Mulifupi mwa chipatacho munali mamita asanu ndi awiri ndipo mulifupi mwa makoma ake munali mamita awiri mbali zonse. Mulitali mwa khonde munali mamita khumi, mulifupi mwake munali mamita asanu ndi limodzi kuchokera kutsogolo mpaka kumbuyo. Panali makwerero khumi, ndipo mbali zonse kunali nsanamira.
Ndipo munthuyo anapita nane mʼchipinda chopatulika cha Nyumba ya Mulungu ndipo anayeza khonde lake; mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu mbali iliyonse kutalika kwake. Mulifupi mwa khomo munali motalika mamita asanu. Makoma a mbali zonse anali a mamita awiri ndi theka mulifupi mwake. Anayezanso kutalika kwa chipinda chopatulika chija ndipo mulitali mwake munali motalika mamita makumi awiri ndi mulifupi mwake munali mamita khumi.
Kenaka munthuyo anakalowa mʼkati ndipo anayeza khonde la pa khomo; khondelo linali mita imodzi mulifupi mwake. Mulifupi mwa khondelo munali mamita atatu. Ndiponso anayeza kutalika kwa chipinda chopatulika chenichenicho. Mulitali mwake munali mamita khumi, ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi. Munthuyo anandiwuza kuti, “Ichi ndicho chipinda chopatulika kwambiri.”
Tsono munthuyo anayeza khoma la Nyumba ya Mulungu; kuchindikira kwake kunali mamita atatu. Panalinso zipinda zina kuzungulira Nyumba ya Mulungu ndipo chilichonse chinali cha mamita awiri mulifupi wake. Zipindazo zinali zitatu zosanjikizana. Chigawo chilichonse chinali ndi zipinda makumi atatu. Pa makoma a Nyumba ya Mulungu panali zochirikiza zipindazo kuti zisatsamire khoma la Nyumba ya Mulungu. Zipinda za mʼmbalizo zinkapita zikulirakulira pomakwera chipinda ndi chipinda potsata kukulirakulira kwa zochirikiza za zipinda zija. Pambali pa Nyumba ya Mulungu panali makwerero okwerera pamwamba, kuchokera chigawo chapansi kudzera chapakati, mpaka kukafika pamwamba.
Ndinaona chiwundo kuzungulira Nyumba ya Mulungu. Chinapanga maziko a zipindazo ndipo chinali cha mamita atatu. Khoma lakunja la zipindazo linali la mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake. Pakati pa chiwundocho ndi zipinda za Nyumba ya Mulungu panali bwalo limeneli la mamita khumi kupingasa kwake kuzungulira Nyumba yonse ya Mulungu. Zitseko za zipinda zamʼmbalizo zinali zotsekulira ku chiwundo. Chitseko chimodzi chinkayangʼana kumpoto ndipo china chinkayangʼana kummwera. Chiwundo chosamangapo kanthu chinali mamita awiri ndi theka kukula kwake kuzungulira ponseponse.
Nyumba imene inali chakummwera moyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu inali mamita 35 mulifupi mwake. Khoma la nyumbayo linali mamita awiri ndi theka kuchindikira kwake kuzungulira ponseponse, ndipo mulitali mwake linali mamita 45.
Ndipo munthuyo anayeza Nyumba ya Mulungu ndipo mulitali mwake inali mamita makumi asanu. Nyumbayo ndi makoma ake, zonse zinali za mamita makumi asanu. Kumaso kwa Nyumba ya Mulungu chakummawa kwa bwalolo mulifupi mwake munali mamita makumi asanu.
Kenaka anayeza kutalika kwa nyumba yoyangʼanana ndi bwalo chakumadzulo kwa Nyumba ya Mulungu, kuphatikizapo njira zamʼkati ku mbali iliyonse. Kutalika kwake kunali mamita makumi asanu.
Chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, chimene chili chamʼkati, khonde lamʼkati loyangʼanana ndi bwalo, mazenera ndi maferemu ake, zonsezi zinali zokutidwa ndi matabwa. Pamwamba moyangʼanana ndi chiwundo, Nyumba ya Mulungu inakutidwa ndi matabwa kuyambira pansi mpaka ku mazenera, (mazenerawo anali okutidwa), pamwamba pa khomo lolowera ku malo opatulika amʼkati komanso kuzungulira makoma onse kunja ndi mʼkati, anajambulapo zithunzi za kerubi mmodzi atakhala pakati pa kanjedza muwiri. Kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri: imodzi inali nkhope ya munthu yoyangʼana kanjedza mbali imodzi, ndi ina inali nkhope ya mkango yoyangʼana kanjedza mbali ina. Zinajambulidwa kuzungulira Nyumba ya Mulungu yonse. Motero kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo komanso pa makoma onse a chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu, anajambula zithunzi za akerubi ndi kanjedza pa makoma onse a malo opatulika.
Mphuthu za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu kutalika kwake mbali zonse kunali kofanana. Ndipo kumaso kwa malo opatulika kunali chinthu china chooneka ngati guwa lansembe la matabwa. Msinkhu wake unali mita imodzi ndi theka, mulitali mwake munali mita imodzi, mulifupi mwake munalinso mita imodzi. Mphuthu zake, tsinde lake ndi mbali zonse zinali za matabwa. Munthuyo anandiwuza kuti, “Tebulo limeneli ndilo limakhala pamaso pa Yehova.” Chipinda chachikulu chija chinali ndi zitseko ziwiri. Malo opatulika aja analinso ndi zitseko ziwiri. Chitseko chilichonse chinali ndi zigawo ziwiri zopatukana. Ndipo pa zitsekopo anajambulipo zithunzi za akerubi ndi kanjedza monga zomwe anajambulapo pa makoma. Kunja kwake kunali ngati denga lamatabwa pamwamba pa khonde lamʼkati. Pa mbali zonse za khonde lamʼkatilo panali mazenera, ndipo pa makoma ake onse anajambulapo zithunzi za kanjedza.
Zipinda za Ansembe
Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku bwalo lakunja chakumpoto ndipo anafika nane ku zipinda zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ina yakumpoto. Nyumba yakumpotoyi mulitali mwake munali mamita makumi asanu, mulifupi mwake munali mamita 25. Panali midadada iwiri, umodzi umayangʼanana ndi bwalo lamʼkati la mamita khumi, winawo umayangʼanana ndi bwalo lakunja. Midadada iwiriyi inali ya nyumba zitatu zosanjikana ndipo imayangʼanana. Kumaso kwa zipindazo kunali njira yamʼkati, mulifupi mwake munali mamita asanu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. Makomo ake analoza chakumpoto. Zipinda zammwamba zinali zazifupi mʼmimbamu kupambana zipinda zamʼmunsi ndi zipinda zapakati chifukwa njira zake zinatenga malo ambiri. Popeza zipinda zinali zosanjikizana katatu ndipo zinalibe nsanamira monga za mabwalo, motero zipinda zamʼmwamba zinali zochepa kuyerekeza ndi zipinda zapansi ndi zipinda zapakati. Panali khoma lakunja lomwe limatsatana ndi zipindazo kutsogolo kwake pambali pabwalo lakunja, kutalika kwake kunali mamita 25. Zipinda za mʼmbali mwa bwalo lakunja mulitali mwake munali mamita 25. Koma zomwe zinali mʼmbali mwa Nyumba ya Mulungu, mulitali mwake munali mamita makumi asanu. Pansi pa zipinda zimenezi panali khomo chakummawa kuchokera ku bwalo lakunja kumene khoma lake linkayambira.
Mbali yakummwera kuyangʼanana ndi bwalo ndi nyumbayo kunali zipinda zina. Kumaso kwa zipindazi kunali njira. Zipindazi mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso maonekedwe ake onse zinali zofanana ndi zipinda zoyangʼana zakumpoto zija. Makomo ndi zitseko zake zinalinso zofanana ndi makomo a zipinda zakummwera. Kunali khomo mʼmbali ya kummawa kumene ankalowerako. Kunalinso khoma logawa zipinda.
Ndipo munthuyo anandiwuza kuti, “Zipinda zakumpoto ndi zakummwera zoyangʼanana ndi bwalo la Nyumba ya Mulungu ndi zoyera. Mʼmenemo ansembe amene amakhala pafupi ndi Yehova amadyeramo zopereka zopatulika kwambiri. Mʼmenemo adzayikamo zopereka zopatulika kwambiri, zopereka za chakudya, nsembe zopepesera machimo ndi nsembe zopepesera kupalamula, poti malowo ndi opatulika. Pamene ansembe alowa ku malo opatulikawa, asatuluke kupita ku bwalo lakunja popanda kusiya momwemo zovala zimene anavala potumikira zija, pakuti zovalazi ndi zopatulika. Avale kaye zovala zina ndipo akhoza kufika kwa anthu.”
Munthuyo atamaliza kuyeza zimene zinali mʼkati mwa Nyumba ya Mulungu, anatuluka nane pa chipata chakummawa ndi kuyeza bwalo lonse. Anayeza mbali yakummawa ndi ndodo yake yoyezera; kutalika kwake kunali mamita 250. Anayeza mbali ya kumpoto ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250. Munthuyo anayeza mbali yakummwera; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake. Kenaka anatembenukira ku mbali ya kumadzulo ndi kuyeza ndi ndodo yake; kutalika kwake kunali mamita 250 atayeza ndi ndodo yake. Motero anayeza mbali zonse zinayi. Panali khoma lozungulira bwalolo mulitali mwake munali mamita 250 ndipo mulifupi mwake munalinso mamita 250. Khomalo linali lolekanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba.
Ulemerero Ubwerera Mʼnyumba ya Mulungu
Pambuyo pake munthuyo anapita nane ku chipinda choyangʼana kummawa, ndipo ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Israeli ukubwera kuchokera kummawa. Liwu lake linali ngati mkokomo wamadzi, ndipo dziko linawala ndi ulemerero wake. Masomphenya amene ndinawaonawa anali ngati masomphenya amene ndinawaona pamene Yehova anabwera kudzawononga mzinda ndiponso ngati masomphenya amene ndinawaona ku mtsinje wa Kebara. Ndipo ndinadzigwetsa chafufumimba. Ulemerero wa Yehova unalowa mʼNyumba ya Mulungu kudzera pa chipata choyangʼana kummawa. Tsono Mzimu unandinyamula nundilowetsa mʼbwalo lamʼkati, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza Nyumba ya Mulungu.
Munthuyo ali chiyimire pambali panga, ndinamva wina akundiyankhula kuchokera mʼNyumba ya Mulungu. Iye anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga waufumu, ndi malo opondapo mapazi anga. Pano ndiye pamene ndidzakhala pakati pa Aisraeli mpaka muyaya. Aisraeliwa kapena mafumu awo sadzayipitsa dzina langa popembedza milungu ina kapena poyika mitembo ya mafumu awo ku zitunda zachipembedzo. Ankamanga chiwundo chawo pafupi ndi chiwundo changa, ndiponso mphuthu zawo pafupi ndi mphuthu zanga, nʼkungokhala khoma chabe pakati pa iwowo ndi Ine. Motero anayipitsa dzina langa loyera ndi machitidwe awo onyansa. Choncho Ine ndinawawononga ndili wokwiya. Tsopano alekeretu kupembedza milungu ina ndipo achotseretu mitembo ya mafumu awo, isakhale pafupi ndi Ine, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo mpaka muyaya.
“Iwe mwana wa munthu, awuze Aisraeliwa za Nyumba ya Mulunguyi, mamangidwe ake ndipo achite manyazi ndi machimo awo, akachita manyazi ndi zoyipa zonse anachita, uwafotokozera za Nyumba ya Mulungu, mamangidwe ake, makomo ake otulukira ndi makomo olowera, ndiye kuti, mamangidwe ake onse. Uwafotokozerenso malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe akuona kuti athe kuwasunga ndi kuwachita.
“Limeneli ndi lamulo la Nyumba ya Mulungu imene idzamangidwe pamwamba pa phiri. Malo ake onse ozungulira adzakhala oyera kwambiri. Limeneli ndilo lamulo la Nyumba ya Mulungu.
Guwa la Nsembe
“Miyeso ya guwa lansembe ndi iyi: Pa tsinde pake padzakhala ngalande ya masentimita makumi asanu kuzama kwake ndi mulifupi mwake. Mʼphepete mwa ngalandeyo kuzungulira guwa lonse, mudzakhala mkombero wa masentimita 25. Kuchokera mʼngalande ya pansi padzakhala mpaka pa phaka lapansi mita imodzi, mulifupi mwake theka la mita. Kuchokera pa phaka lalingʼono mpaka pa phaka lalikulu, msinkhu wake ndi mamita awiri, mulifupi mwake ndi masentimita makumi asanu. Malo osonkhapo moto pa guwa, msinkhu wake udzakhala mamita awiri. Pa ngodya iliyonse ya malo osonkhapo motowo panatuluka nyanga imodzi. Malo osankhalapo moto pa guwa lansembe miyeso yake ndi yofanana mbali zonse. Mulitali mwake mudzakhala mamita asanu ndi limodzi ndipo mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi limodzi. Phaka lapamwamba muyeso wake udzakhala wofanana mbali zonse. Mulitali mudzakhala mamita asanu ndi awiri ndiponso mulifupi mwake mudzakhalanso mamita asanu ndi awiri. Mkombero wake udzakhala wa masentimita 25 ndiponso ngalande yake yozungulira idzakhala ya masentimita 25. Makwerero a guwa lansembe adzayangʼana kummawa.”
Kenaka munthuyo anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Ambuye Yehova akuti: Guwalo litamangidwa, tsono malamulo awa azidzatsatidwa popereka nsembe zopsereza ndiponso powaza magazi pa guwapo. Udzawapatse ansembe, omwe ndi Alevi, a banja la Zadoki, amene amabwera pafupi nane kudzanditumikira, mwana wangʼombe wamwamuna kuti aperekere nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Udzatengeko magazi ake ena ndi kuwapaka pa nyanga zinayi za pa guwa lansembe, pa ngodya zinayi za phaka ndiponso mozungulira mkombero wonse. Motero udzaliyeretsa ndi kulipatula. Udzatenge ngʼombe yayimuna yomwe yaperekedwa ngati nsembe yopepesera machimo, ndipo udzayiwotche pa malo ake enieni mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu, kunja kwa malo opatulika.
“Mmawa mwake udzatenge mbuzi yopanda chilema kuti nayonso iperekedwe ngati nsembe yopepesera machimo. Pambuyo pake idzayeretse guwa lansembe monga unachitira ndi ngʼombe yayimuna ija. Utatha kuyeretsa guwa lansembelo, udzatenge mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndiponso nkhosa yayimuna yopanda chilema. Udzapereke zonsezi pamaso pa Yehova, ndipo ansembe adzazithire mchere ndi kuzipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.
“Kwa masiku asanu ndi awiri, uzidzapereka tsiku ndi tsiku mbuzi yayimuna, mwana wangʼombe, ndiponso nkhosa kuti zikhale nsembe zopepesera machimo. Zonsezi zidzakhale zopanda chilema. Kwa masiku asanu ndi awiriwo ansembe adzachite mwambo woyeretsa ndi kupatula guwa lansembelo. Masiku amenewa atatha, kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu, ansembe azipereka nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe. Apo ndidzakulandirani. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
Mfumu, Alevi ndi Ansembe
Munthu uja anabwerera nane ku chipata chakunja kwa malo opatulika, chomwe chimayangʼana kummawa. Chipatacho chinali chotseka. Yehova anandiwuza kuti, “Chipata ichi chikhale chotseka, chisatsekulidwe. Wina asalowerepo chifukwa Yehova, Mulungu wa Israeli walowera pomwepa. Kalonga yekha angathe kukhala mʼmenemo ndi kumadya chakudya pamaso pa Yehova. Iye adzalowere pa njira ya ku khonde lamʼkati ndi kutulukiranso njira yomweyo.”
Kenaka munthuyo anandidzeretsa pa chipata chakumpoto ndipo tinafika kumaso kwa Nyumba ya Mulungu. Nditapenyetsetsa ndinangoona ulemerero wa Yehova utadzaza mʼNyumba ya Mulungu, ndipo ndinadzigwetsa pansi chafufumimba.
Yehova anandiwuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, samala bwino ndipo uyangʼanitsitse ndi kumvetsa bwino zonse zimene ndikuwuze zokhudza malamulo ndi malangizo a Nyumbayi. Usamalitse za amene angalowe ndi kutuluka mʼNyumbayi. Uwuze mtundu wopanduka wa Israeli kuti Ine Ambuye Yehova ndikuti: Inu Aisraeli, andikwana machitidwe anu onyansawo! Munalowetsa alendo osachita mdulidwe mu mtima ndi mʼthupi momwe mʼNyumba yanga ndipotu anayipitsa Nyumba yanga. Pamene inu munkandipatsa chakudya changa ndi magazi omwe kuwonjezera pa zonyansa zanu zonse ndiye kuti munaphwanya pangano langa. Mʼmalo moti muzisamalira zinthu zanga zopatulika, mwayika alendo kuti aziyangʼanira malo anga opatulika. Ambuye Wamphamvuzonse akuti: Palibe mlendo wosachita mdulidwe mu mtima ndi mʼthupi ngakhalenso mlendo amene amakhala pakati pa Aisraeli amene adzalowe mʼmalo anga opatulika.
“Ndiponso Alevi amene anandisiya kutali pa nthawi imene Israeli anasochera potsata mafano, adzalangidwa chifukwa cha tchimo lawo. Adzangokhala atumiki chabe mʼmalo anga opatulika. Azidzayangʼanira zipata za Nyumba ya Mulungu ndi kugwira ntchito kumeneko. Azidzapha nyama za nsembe zopsereza ndi za nsembe zina za anthu. Choncho azidzayimirira pamaso pa anthu nʼkumawatumikira. Iwowa ankatumikira anthu popembedza mafano awo, ndipo anachititsa Aisraeli kugwa mu uchimo. Nʼchifukwa chake Ine ndikulumbira kuti iwowa ayenera kulangidwa chifukwa cha machimo awo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Iwo sayenera kufika pafupi ndi Ine ndi kunditumikira ngati ansembe, kapena kuyandikira chilichonse cha zinthu zanga zopatulika, kapenanso zopereka zanga zopatulika kwambiri. Iwo adzachititsidwa manyazi chifukwa cha machitidwe awo onyansa. Komabe ndidzawayika kuti aziyangʼanira Nyumba yanga ndi kutumikira pa ntchito zake zonse zoyenera kuti zigwiridwe mʼmenemo.
“Koma ansembe, a fuko la Levi, a banja la Zadoki amene ankatumikira mokhulupirika ku malo anga opatulika pa nthawi imene Aisraeli anasochera ndi kundisiya Ine; iwowa adzasendera kwa Ine kudzanditumikira. Adzafika pamaso panga kuti apereke nsembe za mafuta ndi magazi. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Okhawa ndiwo adzalowe ku malo anga opatulika ndi kudzayandikira tebulo langa kuti adzanditumikire. Amenewa okha ndiwo adzasamalire zinthu zanga.
“Pamene alowa ku zipata za bwalo lamʼkati azivala zovala zabafuta. Asamavale chovala china chilichonse cha ubweya wankhosa pamene akutumikira pa zipata za bwalo la mʼkati kapena kunja kwa Nyumba ya Mulungu. Azivala nduwira za bafuta ndi kabudula wabafuta mʼkati. Asavale chilichonse chowachititsa thukuta. Pamene atuluka ndi kupita ku bwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zimene amatumikira nazo, ndipo azisiye zovalazo mu zipinda zopatulika. Pambuyo pake avale zovala zina, kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo ndi zovala zawozo.
“ ‘Ansembe asamamete mpala kapena kusunga tsitsi lalitali kwambiri, koma azingoliyepula. Wansembe asamwe vinyo pamene ali pafupi kulowa mʼbwalo la mʼkati. Iwo asakwatire akazi amasiye kapena osudzulidwa; koma azikwatira anamwali osadziwa mwamuna a fuko la Israeli kapena akazi amasiye a ansembe anzawo. Ansembe aziphunzitsa anthu anga kusiyanitsa pakati pa zinthu zopatulika ndi zinthu wamba, ndiponso pakati pa zinthu zoyenera ndi zosayenera kuperekedwa nsembe.
“ ‘Pakakhala milandu, ansembe azikhala oweruza ndipo agamule milanduyo potsata malamulo anga. Atsate malamulo anga ndi malangizo anga pa za masiku anga onse a chikondwerero. Asamalirenso kuti masiku anga a Sabata akhale oyera.
“ ‘Wansembe asadziyipitse pokhudza munthu wakufa, pokhapokha ngati wakufayo ndi abambo ake kapena amayi ake, mwana wake wamwamuna kapena wamkazi, mʼbale wake kapena mlongo wake wosakwatiwa. Atatha kuyeretsedwa adikirebe masiku asanu ndi awiri kuti ayere ndithu. Pa tsiku lomwe akukalowa mʼbwalo la mʼkati la malo opatulika kuti akatumikire, apereke nsembe yopepesera machimo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
“ ‘Ansembe asadzakhale ndi cholowa chilichonse ayi. Cholowa chawo ndi Ine. Musadzawapatse chuma mu Israeli; Ine ndidzakhala chuma chawo. Iwo azidzadya nsembe ya chakudya, nsembe yopereka chifukwa cha tchimo ndi nsembe yopepesera machimo. Zinthu zonse zoperekedwa kwa Yehova mu Israeli zidzakhala zawo. Zabwino za zipatso zanu zoyambirira kucha ndiponso mphatso zanu zonse zapadera zidzakhala za ansembe. Inu muziwapatsa chigawo choyamba cha ufa wanu kuti pa nyumba panu pakhale madalitso. Ansembe sayenera kudya kalikonse kofa kokha, kaya mbalame, kapena nyama. Kapena yochita kujiwa.’ ”
Magawidwe a Dziko
“ ‘Mukamadzagawa dziko kuti fuko lililonse lilandire cholowa chake, mudzapatuleko chigawo chimodzi kuti chikhale cha Yehova. Mulitali mwake mudzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita khumi. Malo onsewo adzakhale opatulika. Mʼkati mwa chigawo chimenechi, malo a mamita 250 mbali iliyonse adzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Pozungulira pake ponse padzakhala malo a mamita 25. Mʼchigawo chopatulikacho muyeze malo a makilomita 12 ndi theka mulitali mwake, makilomita asanu mulifupi mwake. Pamenepo padzakhala malo opatulika kwambiri. Malo opatulika amenewa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Yehova kuti amutumikire. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zawo ndi malo omangapo Nyumba ya Mulungu. Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi malo a makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake ndi makilomita asanu mulifupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhale midzi yawo.
“ ‘Moyandikana ndi malo opatulika, padzakhale malo a makilomita awiri ndi theka mulifupi mwake ndi makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake; kuti akhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhala a Aisraeli onse.
“ ‘Mfumu idzakhale ndi malo okhudzana ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda. Malowo ayandikane ndi zigawozo chakummawa ndi chakumadzulo. Malowo atalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israeli kuyambira ku malire akummawa mpaka ku malire akumadzulo. Malowa adzakhala chigawo cha mfumu mu Israeli. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzidzalola Aisraeli kuti akhale ndi zigawo zawozawo.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsono pakwana, inu akalonga a Israeli. Lekani nkhanza zanu ndi kupondereza anthu anga. Muzitsata chilungamo ndi kuchita zokomera anthu. Musapirikitse anthu anga mʼdzikomo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Miyeso yanu yoyezera zinthu monga efa ndi bati zizikhala zokhulupirika. Efa ndi bati ikhale miyeso yolingana kukula kwake. Muyeso wa homeri ukhale wokwanira mabati khumi, ukhalenso wokwanira maefa khumi. Ndiye kuti kukula kwa miyeso iwiriyo kuzidzatsata kukula kwa homeriyo. Muyeso wa sekeli ukhale wokwanira magera makumi awiri. Muyeso wa mina ukhale wolemera masekeli 60.
Zopereka ndi Masiku Achikondwerero
“ ‘Zopereka zomwe mudzidzapereka ndi izi: chimodzi mwa zigawo 60 za tirigu, barelenso chimodzimodzi ndiponso gawo limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, kulitapa pa barele wa homeri. Gawo loyenera la mafuta, loyezedwa ndi bati, ndiponso chigawo mwa zigawo 100 za mafuta. Miyeso yake ili motere: mabati khumi afanana ndi homeri imodzi kapena kori imodzi. Muperekenso nkhosa imodzi pa gulu lankhosa 200 za pa msipu wabwino wa mu Israeli. Izi zidzagwiritsidwa ntchito monga nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano ndi nsembe zopepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Yehova. Anthu onse a mʼdzikomo azidzapereka zimenezi kwa mfumu ya Israeli. Udzakhala udindo wa mfumu kupereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, ndi nsembe za zakumwa pa nthawi ya zikondwerero, chikondwerero cha mwezi watsopano ndi cha masabata, nthawi yonse ya zikondwerero zoyikika za Aisraeli. Mfumuyo idzapereka nsembe zopepesera machimo, nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe zopepesera machimo a Aisraeli.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba muzitenga mwana wangʼombe wamwamuna wopanda chilema ndi kuchita mwambo woyeretsa malo opatulika. Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo ndipo awapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinayi za pamwamba pa guwa lansembe ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo la mʼkati. Muzichita chimodzimodzi pa tsiku la chisanu ndi chiwiri la mwezi, kuchitira aliyense amene wachimwa mosafuna kapena mosadziwa. Motero Nyumba ya Mulungu idzakhala yoyera.
“ ‘Pa tsiku la 14 la mwezi woyamba muzichita chikondwerero cha Paska, chikondwerero chake cha masiku asanu ndi awiri. Pa masiku amenewo muzidzadya buledi wopanda yisiti. Pa tsiku loyamba la chikondwererocho, mfumu ipereke nsembe ya ngʼombe yayimuna monga nsembe yopepesera machimo ake ndi machimo a anthu onse a mʼdziko. Pa masiku asanu ndi awiri a chikondwererocho, mfumu ipereke kwa Yehova nsembe zopsereza izi: ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, zonsezi zopanda chilema. Pa masikuwa mfumu iziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo. Pamodzi ndi ngʼombe iliyonse yayimuna ndi nkhosa iliyonse yayimuna, mfumu ipereke chopereka cha chakudya chokwanira efa imodzi ndiponso mafuta okwanira hini imodzi pa efa iliyonse.
“ ‘Pa nthawi ya chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri, chimene chimayamba pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mfumuyo iziperekanso nsembe za mtundu womwewo: nsembe zopepesera machimo, nsembe zopsereza, nsembe za chakudya ndi za mafuta.’ ”
“Ambuye Yehova akuti, Chipata chakummawa cha bwalo lamʼkati chizikhala chotseka pa masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito, koma chizitsekulidwa pa tsiku la sabata ndi pa tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Mfumu izilowa podzera mʼkhonde la mʼkati la chipata pochokera kunja, nʼkudzayima pafupi ndi nsanamira yapakhomo. Ansembe apereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano. Mfumuyo ipembedze pa chiwundo cha pa chipatacho kenaka nʼkutuluka. Koma chipatacho asachitseke mpaka madzulo. Anthu a mʼdziko azipembedza pamaso pa Yehova pa khomo la chipata chimenechi pa masiku a sabata ndi pa tsiku la mwezi watsopano. Nsembe yopsereza imene mfumu iyenera kupereka kwa Yehova ikhale motere: pa tsiku la Sabata izipereka ana ankhosa aamuna asanu ndi mmodzi wopanda chilema, ndiponso nkhosa yayima yopanda chilema. Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, mfumu izipereka nsembe ya chakudya yokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi ana ankhosa, mfumu izipereka monga ikufunira kutero. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya tirigu. Pa tsiku la mwezi watsopano mfumuyo ipereke mwana wangʼombe wamwamuna, ana ankhosa asanu ndi mmodzi ndiponso nkhosa yayimuna, zonsezi zopanda chilema. Ipereke efa imodzi ya tirigu pa ngʼombe yayimuna iliyonse ndiponso efa ina pa nkhosa yayimuna iliyonse. Pa ana ankhosa ipereke tirigu monga ikufunira kutero. Pamodzi ndi efa ya tirigu, ipereke hini imodzi ya mafuta. Pamene mfumu ikulowa, izidzera mʼkhonde lamʼkati la chipata chakummawa, izitulukiranso pomwepo.
“Anthu a mʼdzikomo akabwera kudzapembedza Yehova pa masiku a chikondwerero, ngati munthu alowera pa chipata chakumpoto atulukire chipata chakummwera. Munthu wolowera chipata chakummwera, atulukire chipata chakumpoto. Munthu asatulukire pomwe walowera, koma atulukire pa chipata choyangʼanana nacho. Mfumu izidzakhala pakati pawo. Anthu akamadzalowa mfumu idzalowa nawo. Anthu akamadzatuluka mfumu idzatuluka nawo.
“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse. Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho.
“Tsiku lililonse nthawi ya mmawa azipereka kwa Yehova mwana wankhosa wa chaka chimodzi. Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo. Motero azipereka mwana wankhosa ndi chopereka cha chakudya ndi mafuta mmawa uliwonse kuti zikhale nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku.
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ngati kalonga apereka mphatso chigawo cha cholowa chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo idzakhala ya ana akewo. Idzakhala yawo chifukwa ndi cholowa chawo. Koma ngati ipereka mphatso yotere kuchokera pa cholowa chake kwa mmodzi mwa antchito ake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka chaufulu. Pambuyo pake idzabwereranso kwa kalongayo chifukwa cholowa chake ndi cha ana ake. Kalonga asalande cholowa chilichonse cha anthu, kuwachotsa mʼdera lawo la dziko. Iye apereke kwa ana ake cholowa chawo chochokera pa chuma chakechake, kuti pasapezeke ndi mmodzi yemwe mwa anthu anga wolandidwa chuma chake.’ ”
Kenaka munthu uja anandidzeretsa pa khomo la pambali pa chipata nandilowetsa ku zipinda za ansembe zoyangʼana kumpoto. Ndipo ndinaona kumeneko malo chakumadzulo kwa zipindazo. Munthuyo anandiwuza kuti, “Awa ndi malo amene ansembe adzaphikirapo nsembe yopepesera kupalamula ndi nsembe yopepesera machimo. Kumenekonso azidzawotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi mʼbwalo lakunja kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu ena.”
Pambuyo pake anandilowetsa mʼbwalo lakunja napita nane ku ngodya zinayi za bwalolo. Ndipo ndinaona mʼkati mwa ngodya iliyonse bwalo lina. Motero pa ngodya zinayi za bwalo panalinso mabwalo ena angʼonoangʼono. Mabwalo amenewa anali ofanana. Mulitali mwake munali mamita makumi awiri ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi ndi asanu. Kuzungulira mabwalo anayi angʼonoangʼono aja panali mpanda wamiyala, ndi malo asonkhapo moto omangidwa mʼmunsi mwa mpandawo mozungulira. Munthuyo anandiwuza kuti, “Izi ndi zipinda zophikiramo. Mʼmenemu anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzaphikiramo nyama za nsembe za anthu.”
Mtsinje Wotuluka Mʼnyumba ya Mulungu
Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe. Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.
Munthuyo anapita chakummawa ali ndi chingwe choyezera mʼdzanja lake. Iye anayeza mamita 500, ndipo pambuyo pake analowa nane mʼmadziwo amene ankalekeza mʼkakolo. Anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼmawondo. Iye anayezanso mamita 500 ndipo analowa nane mʼmadzi amene amalekeza mʼchiwuno. Munthuyo anayezanso mamita 500, ndipo madziwo anasanduka mtsinje woti sindikanatha kuwoloka, pakuti madziwo anakwera, ndipo anali ozama ofunika kusambira pofuna kuwoloka. Munthuyo anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuziona zimenezi?”
Kenaka anabwerera nane ku gombe la mtsinjewo. Nditafika pa gombepo, ndinaona mitengo yambiri ku mbali iliyonse ya mtsinjewo. Tsono munthuyo anandiwuza kuti, “Madziwa akupita ku chigawo chakummawa ndi kutsikira ku chigwa cha Araba. Kenaka akathira mʼNyanja Yakufa, ndipo akakalowa mʼnyanjayo, madzi a nyanjayo adzasanduka okoma. Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo. Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu. Koma mathawale ake ndi maiwe ake sadzakhala ndi madzi abwino; adzakhala ndi madzi a mchere. Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”
Malire a Dziko
Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri. Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu.
“Malire a dzikolo adzakhala motere:
Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi, Berota ndi Sibraimu (mizinda imene ili pakati pa malire a Damasiko ndi Hamati mpaka kukafika ku Hazeri Hatikoni mzinda umene uli mʼmalire mwa Haurani. Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto.
Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa.
Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera.
Mbali ya kumadzulo, malire adzakhala Nyanja Yayikulu mpaka pa malo oyangʼanana ndi Lebo Hamati. Awa adzakhala malire akumadzulo.”
“Mugawane dziko limeneli pakati panu potsata mafuko a Israeli. Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli. Mu fuko lililonse kumene mlendoyo akukhala mumupatse cholowa chake.” Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Magawidwe ka Dziko
“Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.
“Aseri adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Dani kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Nafutali adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Aseri kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Manase adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Nafutali kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Efereimu adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi dziko la Manase kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Rubeni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Efereimu kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Yuda adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi Rubeni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Kuchita malire ndi Yuda kuchokera kummawa mpaka kumadzulo padzakhala chigawo chimene mudzachipereke ngati mphatso yapadera. Mulifupi mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulitali mwake, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo, mudzafanana ndi zigawo zina za mafuko. Malo a Nyumba ya Mulungu adzakhala pakati pake.
“Chigawo chapadera chimene mudzachipereke kwa Yehova mulitali mwake mudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu. Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera. Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.
“Moyandikana ndi chigawo cha ansembe, Alevi adzakhala ndi dera lawo lotalika makilomita khumi ndi awiri ndi theka, ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Kutalika kwake konse kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita asanu. Asagulitse kapena kusinthitsa mbali iliyonse ya chigawo chimenechi. Ichi ndi chigawo chabwino kwambiri ndipo chisapatsidwe kwa anthu ena, chifukwa ndi chopatulikira Yehova.
“Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati. Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250. Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125. Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda. Anthu ogwira ntchito mu mzinda amene adzalime mʼmundamo adzachokera ku mafuko onse a Israeli. Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.
“Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu. Choncho chigawo cha Alevi ndi chigawo cha mzinda zidzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo kwa dziko la Benjamini.
“Za mafuko ena otsala zidzayenda motere: Benjamini adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzayambira mbali ya kummawa mpaka ya kumadzulo.
“Simeoni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Benjamini kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Isakara adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Simeoni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Zebuloni adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Isakara kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Gadi adzakhala ndi chigawo chimodzi. Chidzachita malire ndi chigawo cha Zebuloni kuchokera kummawa mpaka kumadzulo.
“Malire a Gadi a mbali yakummwera ku Negevi adzayenda kuchokera ku Tamara mpaka ku dziwe la Meriba Kadesi komanso kuchokera ku Mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu.
“Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Zipata za Mzinda
“Izi ndizo zidzakhale zipata zotulukira mzinda, ndipo zidzatchulidwa mayina a mafuko a Israeli. Kuyambira kumpoto kumene kudzakhala kotalika mamita 2,250, kudzakhale zipata zitatu izi: cha Rubeni, cha Yuda ndi cha Levi.
“Mbali ya kummawa, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Yosefe, chipata cha Benjamini ndi chipata cha Dani.
“Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.
“Mbali ya kumadzulo, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250 kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Gadi, chipata cha Aseri ndi chipata cha Nafutali.
“Choncho kutalika kwa mzinda kuzungulira kwake kudzakhala mamita 9,000.
“Ndipo dzina la mzindawo kuyambira nthawi imeneyo mpaka mʼtsogolo lidzakhala:
Yehova Ali Pano.”