- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 EKSODO Eksodo Eksodo Ekso Eksodo Aisraeli Azunzidwa ku Igupto Awa ndi mayina a ana a Israeli amene anapita ku Igupto pamodzi ndi Yakobo abambo awo, aliyense ndi banja lake: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda; Isakara, Zebuloni, Benjamini; Dani, Nafutali; Gadi ndi Aseri. Anthu onse obadwa mwa Yakobo analipo 70. Yosefe nʼkuti ali kale ku Igupto. Tsono Yosefe ndi abale ake onse ndiponso mʼbado wawo wonse anamwalira. Koma Aisraeli anaberekana ndi kuchuluka kwambiri nakhala amphamvu kwambiri, kotero kuti anadzaza dzikolo. Pambuyo pake mfumu yatsopano imene sinkamudziwa Yosefe, inayamba kulamulira dziko la Igupto. Iyo inati kwa anthu ake, “Taonani, Aisraeli achuluka ndipo ndi amphamvu kwambiri kuposa ife. Tiyeni tiwachenjerere. Tikapanda kutero adzachuluka kuposa ife, ndipo ngati kutakhala nkhondo, adzadziphatika kwa adani athu nadzamenyana nafe, kenaka nʼkudzachoka mʼdziko muno.” Kotero anayika akapitawo kuti aziwazunza ndi kuwagwiritsa ntchito yolemetsa mokakamiza. Iwo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramesesi kumene ankasungirako chakudya. Koma pamene ankawazunza kwambiri, Aisraeli ndiye ankachulukirachulukira mpaka kubalalikira mʼdziko lonse. Kotero Aigupto anayamba kuopa Aisraeliwo ndipo anawagwiritsa ntchito mwankhanza kwambiri. Aigupto anachititsa moyo wa Aisraeli kukhala owawa kwambiri powagwiritsa ntchito yakalavulagaga yowumba njerwa ndi kuponda dothi lomangira, pamodzi ndi ntchito zina zosiyanasiyana zamʼminda. Iwo anakakamiza Aisraeli mwankhanza kuti agwire ntchito yowawayi. Azamba Akana Kumvera Mfumu Mfumu ya Igupto inati kwa azamba a Chihebri omwe mayina awo anali Sifira ndi Puwa, “Mukamathandiza amayi a Chihebri pa mwala wochirira, muzionetsetsa kuti akabadwa mwana wamwamuna muzipha, koma akakhala wamkazi muzimuleka akhale ndi moyo.” Koma azambawo ankaopa Mulungu ndipo sanachite zimene mfumu ya Igupto inawawuza kuti achite. Iwo analeka ana aamuna kuti akhale ndi moyo. Kenaka mfumu ya Igupto inayitanitsa azamba aja ndi kuwafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwachita zimenezi? Bwanji mwasiya ana aamuna kuti akhale ndi moyo?” Azambawo anamuyankha Farao kuti, “Amayi a Chihebri sali ngati amayi a Chiigupto; Iwo ndi amphamvu ndipo amachira azamba asanafike.” Kotero Mulungu anawakomera mtima azambawo, ndipo Aisraeli anapitirirabe kuchulukana nakhala amphamvu kwambiri. Pakuti azambawo ankaopa Mulungu, Iye anawapatsa mabanja awoawo. Pamenepo Farao analamulira anthu ake onse kuti, “Mwana wamwamuna aliyense akabadwa, mukamuponye mu mtsinje wa Nailo, koma wamkazi mulekeni akhale ndi moyo.” Kubadwa kwa Mose Ndipo munthu wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi wa fuko lomwelo. Mkaziyo anatenga pathupi ndipo anabereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo anali wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu. Koma mwanayo atafika pa msinkhu woti sakanathanso kubisidwa, amayi ake anatenga kadengu kopangidwa ndi bango nakamata phula. Kenaka anayika mwanayo mʼmenemo ndi kukamuyika pa mabango mu mtsinje wa Nailo. Mlongo wake wa mwanayo anayima pataliko kuti aone chimene chidzamuchitikira mwanayo. Mwana wamkazi wa Farao anapita ku mtsinje wa Nailo kukasamba ndipo adzakazi ake ankayenda mʼmbali mwa mtsinjewo. Tsono mwana wa Farao uja anaona kadenguko pakati pa mabango ndipo anatuma mdzakazi wake kuti akakatenge. Iye atavundukula anaona mwana wamwamuna akungolira. Iye anamva naye chisoni mwana uja, nati, “Ameneyu ndi mmodzi mwa ana a Chihebri.” Kenaka mlongo wake wa mwanayo anafunsa mwana wa Farao kuti, “Ndingapite kukakupezerani mmodzi mwa amayi a Chihebri kuti azikakulererani mwanayu?” Iye anayankha kuti, “Inde, pita.” Ndipo mtsikanayo anapita nakayitana amayi a mwanayo. Mwana wa Farao anati, “Tengani mwanayu mukandilerere, ndidzakulipirani.” Mayiyo anatenga mwanayo kukamulera. Mwanayo atakula anakamupereka kwa mwana wa Farao ndipo anakhala mwana wake. Iye anamutcha dzina lake Mose, popeza anati, “Ndinamuvuwula mʼmadzi.” Mose Athawira ku Midiyani Tsiku lina, Mose atakula, anapita kumene kunali anthu a mtundu wake ndipo anawaona akugwira ntchito yowawa. Iye anaona Mwigupto akumenya Mhebri, mmodzi mwa anthu a mtundu wake. Atayangʼana uku ndi uku, naona kuti panalibe wina aliyense, Mose anamupha Mwiguptoyo ndipo anamukwirira mu mchenga. Mmawa mwake Mose anapita ndipo anaona anthu awiri a Chihebri akumenyana. Iye anafunsa amene anali wolakwa kuti, “Chifukwa chiyani ukumenya Mhebri mnzako?” Munthu uja anati, “Kodi ndani anakuyika kuti ukhale wotilamulira ndi wotiweruza? Kodi ukufuna kundipha monga momwe unaphera Mwigupto uja?” Mose anachita mantha ndipo anati mu mtima mwake, “Chimene ndinachita chija chadziwika.” Farao atamva zimenezi anafuna kuti aphe Mose, koma Mose anathawa ndipo anapita kukakhala ku Midiyani. Ali kumeneko, tsiku lina anakhala pansi pafupi ndi chitsime. Wansembe wa ku Midiyaniko anali ndi ana aakazi asanu ndi awiri. Iwowa anabwera kudzatunga madzi ndi kudzaza mu zomwera kuti amwetse nkhosa za abambo awo. Koma kunabwera abusa ena amene anathamangitsa atsikana aja. Ndiye Mose anayimirira nawathandiza atsikana aja ndi kumwetsa nkhosa zawo. Atsikana aja atabwerera kwa abambo awo Reueli, iye anawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani lero mwabwera msanga?” Atsikanawo anayankha kuti, “Mwigupto wina ndiye watilanditsa kwa abusa. Ndiponso anatitungira madzi ndi kumwetsa ziweto zathu.” Tsono Reueli anafunsa ana ake kuti, “Ndiye ali kuti munthuyo? Chifukwa chiyani mwamusiya? Kamuyitaneni kuti adzadye.” Mose anavomera kukhala ndi Reueli, ndipo anamupatsa Zipora kuti akhale mkazi wake. Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.” Nthawi yonseyo nʼkuti ana a Israeli akulira chifukwa cha ukapolo wawo uja. Iwo anafuwula kupempha thandizo, ndipo kulira kwawoko kunafika kwa Mulungu. Mulungu anamva kubuwula kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mulungu ataona Aisraeli aja ndi masautso awo, Iye anawamvera chifundo. Kuyitanidwa kwa Mose pa Chitsamba Choyaka Moto Tsono Mose amaweta ziweto za mpongozi wake Yetero, wansembe uja wa ku Midiyani. Tsiku lina iye anazitsogolera kupita ku chipululu ndipo anafika ku phiri la Mulungu lotchedwa Horebu. Kumeneko mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye mʼmalawi amoto mʼchitsamba. Mose anaona kuti ngakhale chitsambacho chimayaka koma sichimanyeka. Tsono Mose anati mu mtima mwake, “Ine ndipita komweko ndikaone zodabwitsazi, chitsamba sichikunyeka chifukwa chiyani?” Yehova ataona kuti Mose anapatuka kuti adzaonetsetse, Mulungu anamuyitana Mose kuchokera mʼchitsambamo nati, “Mose! Mose!” Ndipo anayankha, “Wawa.” Mulungu anati, “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako, pakuti malo amene wayimapo ndi opatulika.” Mulungu anati, “Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo.” Atamva zimenezi, Mose anaphimba nkhope yake chifukwa anaopa kuona Mulungu. Yehova anati, “Ine ndaona ndithu mazunzo a anthu anga amene ali ku Igupto. Ndamva kulira kwawo chifukwa cha anthu amene akuwapsinja, ndipo ndakhudzidwa ndi masautso awo. Choncho ndabwera kuti ndiwapulumutse mʼdzanja la Aigupto, kuwatulutsa mʼdzikolo ndi kukawalowetsa mʼdziko labwino ndi lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi, kwawo kwa Akanaani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Ine ndamva ndithu kulira kwa Aisraeli, ndipo ndaona mmene Aigupto akuwazunzira. Kotero tsopano, pita. Ine ndikukutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga, Aisraeli mʼdziko la Igupto.” Koma Mose anafunsa Mulungu, “Ine ndine yani kuti ndipite kwa Farao ndi kukatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto?” Ndipo Mulungu anati, “Ine ndidzakhala nawe, ndipo ichi chidzakhala chizindikiro kwa iwe kuti ndine amene ndakutuma; Ukadzatulutsa anthu anga mʼdziko la Igupto, udzapembedza Mulungu pa phiri lino.” Mose anati kwa Mulungu, “Ngati ndipita kwa Aisraeli ndi kukawawuza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ ndipo iwo nʼkukandifunsa kuti ‘Dzina lake ndi ndani?’ Tsono ine ndikawawuze chiyani?” Mulungu anati kwa Mose, “NDINE AMENE NDILI. Izi ndi zimene ukanene kwa Aisraeli: ‘NDINE wandituma kwa inu.’ ” Mulungu anatinso kwa Mose, “Ukanene kwa Aisraeli kuti ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo, wandituma kwa inu.’ Ili ndilo dzina langa mpaka muyaya, ndipo mibado ya mʼtsogolomo izidzanditchula ndi dzina limeneli. “Pita, ukawasonkhanitse akuluakulu a Israeli ndipo ukati kwa iwo, ‘Yehova, Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, anandionekera ndipo akuti Iye wadzakuyenderani ndipo waona mmene Aigupto akukuzunzirani. Choncho wanenetsa kuti adzakutulutsani mʼdziko la Igupto, dziko la masautsoli kupita ku dziko la Akanaani, Ahiti, Aamori Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi.’ “Akuluakulu a Israeli akakumvera. Kenaka iwe ndi akuluakuluwo mukapite kwa mfumu ya Igupto ndipo mukanene kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri, wakumana nafe. Tsono tikukupemphani kuti mutilole tipite pa ulendo wa masiku atatu mʼchipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’ Koma Ine ndikudziwa kuti mfumu ya Igupto sikakulolani kuti mupite pokhapokha Ine nditayikakamiza. Tsono Ine ndidzatambasula dzanja langa ndi kukantha Aigupto ndi zodabwitsa zanga zimene ndidzazichita pakati pawo. Zikadzatha izi, Iye adzakulolani kuti mupite. “Ndipo ine ndidzafewetsa mtima wa Aigupto pa anthu anga, kotero kuti mukadzatuluka simudzapita wopanda kanthu. Mkazi aliyense adzapemphe Mwigupto woyandikana naye ndiponso mkazi amene akukhala mʼnyumba yake, kuti amupatse ziwiya za siliva ndi golide ndiponso zovala zimene mudzaveka ana anu aamuna ndi aakazi. Ndipo potero mudzawalanda zonse Aiguptowo.” Mulungu Apatsa Mose Mphamvu Zochita Zodabwitsa Mose anayankha, “Aisraeliwo sakandikhulupirira ndipo sakandimvera. Iwowo adzati, ‘Yehova sanakuonekere iwe.’ ” Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.” Yehova anati, “Tayiponya pansi.” Mose anayiponya pansi ndipo inasanduka njoka ndipo anayithawa. Kenaka Yehova anati kwa iye, “Igwire mtchira.” Ndipo Mose anayigwira mchira njokayo ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake. Yehova anati, “Ukachite zimenezi ndipo akakukhulupirira kuti Yehova, Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo, wakuonekera iwe.” Yehova anatinso, “Pisa dzanja lako mʼmalaya akowo.” Choncho Mose anapisa dzanja lake mʼmalaya ake ndipo pamene analitulutsa, linali la khate kuchita kuti mbuu ngati ufa. Yehova anati, “Tsopano pisanso dzanja lako mʼmalaya.” Mose anapisanso dzanja lakelo mʼmalaya ake ndipo atalitulutsa, linali labwinobwino, ngati thupi lake lonse. Tsono Yehova anati “Akakapanda kukukhulupirira, osalabadira chozizwitsa choyambacho, akakhulupirira ndithu chifukwa cha chozizwitsa chachiwiricho. Koma ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwiri izi kapena kukumvera, ukatunge madzi a mu mtsinje wa Nailo ndi kuwathira pa mtunda powuma ndipo madziwo adzasanduka magazi.” Mose anati kwa Yehova, “Chonde Ambuye, chikhalire ine ndakhala munthu wosatha kuyankhula bwino. Ngakhale tsopano pamene mukundiyankhula, lilime langa ndi lolemera. Ndine wachibwibwi.” Yehova anati kwa iye, “Kodi anapatsa munthu pakamwa ndani? Ndani amasandutsa munthu kuti akhale wosayankhula kapena wosamva? Ndani amapanga munthu kukhala wopenya kapena wosaona? Kodi si Ine Yehova? Tsopano pita, Ine ndidzakuthandiza kuyankhula ndipo ndidzakulangiza zoti ukanene.” Koma Mose anati, “Chonde Ambuye, pepani, tumani wina kuti akachite zimenezi.” Kenaka Yehova anamupsera mtima Mose ndipo anati, “Kodi suli ndi mʼbale wako Aaroni wa fuko la Levi? Ine ndikudziwa kuti iye amayankhula bwino. Iye wanyamuka kale kudzakumana nawe ndipo adzasangalala akadzakuona. Iwe udzayankhula naye ndi kumuwuza mawu oti akanene. Ine ndidzakuthandizani kuyankhula nonse awirinu ndi kukulangizani zoti mukachite. Iye akayankhula kwa anthu mʼmalo mwako. Iye adzakhala wokuyankhulira ndipo iweyo udzakhala ngati Mulungu kwa iye. Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.” Mose Abwerera ku Igupto Tsono Mose anabwerera kwa Yetero, mpongozi wake ndipo anati kwa Iye, “Chonde ndiloleni kuti ndibwerere ku Igupto kwa anthu anga kuti ndikaone ngati ali moyo.” Yeteri anati, “Pitani mu mtendere.” Nthawiyi Yehova anali atamuwuza kale Mose ku Midiyani kuti, “Bwerera ku Igupto, pakuti anthu onse amene amafuna kukupha aja anamwalira.” Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake. Yehova anati kwa Mose, “Ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao zodabwitsa zonse zimene ndayika mphamvu mwa iwe kuti ukachite. Koma Ine ndidzawumitsa mtima wake kotero kuti sadzalola anthuwo kuti apite. Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’ Choncho ndikuti, ‘Mulole mwana wanga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana, Ine ndidzapha mwana wako wachisamba.’ ” Pambuyo pake Mose ali mʼnjira, pamalo wogona, Yehova anakumana naye, ndipo anafuna kumupha. Koma Zipora anatenga mwala wakuthwa nachita mdulidwe mwana wake ndipo khungulo analikhudzitsa pa mapazi a Mose. Iye anati “Zoonadi, kwa ine ndiwe mkwati wamagazi.” Choncho Yehova anamuleka Mose wosamupha. Pa nthawiyo, Zipora anati, “Mkwati wa magazi,” ponena za mdulidwe. Yehova anati kwa Aaroni, “Pita ku chipululu ukakumane ndi Mose.” Iye anapitadi nakakumana ndi Mose pa phiri la Mulungu namupsompsona. Kenaka Mose anamufotokozera Aaroni chilichonse chimene Yehova anamutuma kuti akanene. Anamufotokozera za zizindikiro zozizwitsa zimene anamulamulira kuti akazichite. Mose ndi Aaroni anapita kukasonkhanitsa pamodzi akuluakulu onse a Aisraeli. Ndipo Aaroni anawafotokozera zonse zimene Yehova ananena kwa Mose. Anachita zizindikirozo pamaso pa anthu onse, ndipo anakhulupirira. Iwo atamva kuti Yehova anadzawayendera ndi kuti waona mmene akuzunzikira, anaweramitsa mitu pansi napembedza. Mose Akumana ndi Farao Zitachitika izi, Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndipo anati, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Aloleni anthu anga apite, kuti akachite chikondwerero cha Ine mʼchipululu.’ ” Koma Farao anati, “Yehova ndani kuti ine ndimumvere ndi kulola Aisraeli kuti apite? Ine Yehova sindikumudziwa ndipo sindilola kuti Aisraeli apite.” Ndipo iwo anati, “Mulungu wa Ahebri anakumana nafe. Chonde tiloleni tipite ulendo wa masiku atatu ku chipululu kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, ngati sititero iye adzatipweteka ndi miliri kapena lupanga.” Koma mfumu ya Igupto inati, “Mose ndi Aaroni, chifukwa chiyani mukuchititsa anthuwa kuti asagwire ntchito zawo? Bwererani ku ntchito zanu!” Ndiponso Farao anati, “Taonani, anthuwa mʼdziko muno alipo ochuluka, ndipo inu mukuwaletsa kugwira ntchito.” Njerwa Zopanda Udzu Pa tsiku lomwelo Farao analamulira akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu kuti “Inu musawapatsenso udzu wopangira njerwa monga mumachitira kale, iwo azipita ndi kukatenga udzu wawo. Koma musawachepetsere chiwerengero cha njerwa chomwe munawalamulira kale kuti aziwumba. Iwowa ndi aulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tiloleni tipite tikapereke nsembe kwa Mulungu wathu.’ Muwakhawulitse ndi ntchito anthu amenewa kuti azitanganidwa, asakhale ndi mpata omvera zabodza.” Choncho akapitawo a thangata ndi anzawo a Chiisraeli amene ankayangʼanira anthu anapita kwa anthu aja nati, “ ‘Farao akuti sadzakupatsaninso udzu. Mʼmalo mwake mupite mukadzimwetere udzu kulikonse kumene mungawupeze. Komabe ntchito yanu sichepetsedwa.’ ” Kotero anthuwo anamwazikana mʼdziko lonse la Igupto kukamweta udzu. Akapitawo a thangata aja anawafulumiza anthu aja nati, “Malizani kugwira ntchito yanu ya tsiku ndi tsiku monga mmene zinalili pamene munkapatsidwa udzu.” Akapitawo a thangata a Farao ankawamenya oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja nawapanikiza kuti, “Chifukwa chiyani lero simunawumbe chiwerengero chovomerezeka cha njerwa monga chakale chija?” Pamenepo oyangʼanira anzawo a Chiisraeli aja anapita kukadandaula kwa Farao kuti, “Chifukwa chiyani mwachitira antchito anu zotere? Antchito anu sakupatsidwa udzu, komabe akutiwuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ Antchito anu akumenyedwa, koma cholakwa sichili ndi anthu anu.” Farao anati, “Ulesi, inu ndinu alesi! Nʼchifukwa chake mukumanena kuti, ‘Mutilole tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’ Pitani tsopano kuntchito. Simudzapatsidwanso udzu komabe muyenera kuwumba muyeso wanu wovomerezeka wa njerwa.” Oyangʼanira anzawo a Chiisraeli anazindikira kuti ali pa mavuto pamene anawuzidwa kuti, “Musachepetse chiwerengero cha njerwa chimene muyenera kuwumba tsiku lililonse.” Atachoka pamaso pa Farao, anakumana ndi Mose ndi Aaroni akuwadikira, ndipo iwo anati, “Yehova akupenyeni ndi kukuweruzani popeza mwachititsa Farao ndi nduna zake kuti anyansidwe nafe ndipo mwayika lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.” Mulungu Alonjeza Chipulumutso Mose anabwerera kwa Yehova ndipo anati, “Chonde Ambuye, chifukwa chiyani mukuzunza anthu anu? Kodi munanditumira zimenezi? Chipitireni changa kwa Farao kukamuyankhula mʼdzina lanu, iye wakhala akuzunza anthuwa, ndipo inu simunawapulumutse konse anthu anu.” Yehova anawuza Mose kuti, “Tsopano udzaona zimene ndimuchite Farao: Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzalola anthu anga kuti atuluke. Chifukwa cha dzanja langa lamphamvu adzawatulutsa mʼdziko lake.” Mulungu anatinso kwa Mose, “Ine ndine Yehova. Ndinaonekera kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo monga Mulungu Wamphamvuzonse, koma sindinawadziwitse dzina langa kuti ndine Yehova. Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuwalonjeza kuti ndidzawapatsa dziko la Kanaani kumene anakhalako kale ngati alendo. Ndamvanso kubuwula kwa Aisraeli, amene Aigupto awayesa akapolo ndipo ndakumbukira pangano langa.” “Nʼchifukwa chake nena kwa Aisraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndidzakumasulani mu ukapolo, ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasuka ndi kuchita ntchito zachiweruzo. Ndidzakutengani kukhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Pamenepo inu mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu amene ndinakutulutsani mʼgoli la Aigupto. Ndipo ndidzakufikitsani ku dziko limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo. Ndidzakupatsani dziko limenelo kuti likhale lanu. Ine ndine Yehova.’ ” Mose anawafotokozera Aisraeli zimenezi, koma iwo sanamumvere chifukwa cha kukhumudwa ndi goli lankhanza. Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita ukawuze Farao mfumu ya Igupto kuti awalole Aisraeli atuluke mʼdziko lake.” Koma Mose ananena kwa Yehova kuti, “Ngati Aisraeli sanandimvere, Farao akandimvera chifukwa chiyani, pajatu sinditha kuyankhula bwino?” Mibado ya Mose ndi Aaroni Ndipo Yehova analamula Mose ndi Aaroni kuti awuze Aisraeli ndi Farao mfumu ya Igupto kuti Aisraeli ayenera kutuluka mʼdziko la Igupto. Atsogoleri a mafuko awo anali awa: Ana a Rubeni mwana wachisamba wa Israeli anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karimi. Awa anali mafuko a Rubeni. Ana a Simeoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Saulo mwana wa kwa mkazi wa Chikanaani. Awa anali mafuko a Simeoni. Mayina a ana a Levi pamodzi ndi zidzukulu zawo anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Levi anakhala ndi moyo kwa zaka 137. Ana a Geresoni, mwa mafuko awo, anali Libini ndi Simei. Ana a Kohati anali Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Kohati anakhala ndi moyo zaka 133. Ana a Merari anali Mali ndi Musi. Awa anali mafuko a Levi monga mwa mibado yawo. Amramu anakwatira Yokobedi mlongo wa abambo ake, amene anabereka Aaroni ndi Mose. Amramu anakhala ndi moyo kwa zaka 137. Ana a Izihari anali Kora, Nefegi ndi Zikiri. Ana a Uzieli anali Misaeli, Elizafani ndi Sitiri. Aaroni anakwatira Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wa Nasoni ndipo Iye anabereka Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. Ana a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu. Awa ndiwo mafuko a Kora. Eliezara mwana wa Aaroni anakwatira mmodzi mwa ana aakazi a Putieli, ndipo anabereka Finehasi. Awa anali atsogoleri a mabanja a Levi, monga mwa mafuko awo. Aaroni ndi Mose ndi aja amene Yehova anawawuza kuti, “Tulutsani Aisraeli mu Igupto mʼmagulu awo.” Mose ndi Aaroni ndiwo amene anayankhula ndi Farao mfumu ya Igupto kuti atulutse Aisraeli mu Igupto. Aaroni Ayankhula Mʼmalo mwa Mose Tsopano pamene Yehova anayankhula kwa Mose mu Igupto, anati, “Ine ndine Yehova. Umuwuze Farao mfumu ya Igupto zonse zimene Ine ndikuwuze iwe.” Koma Mose anati kwa Yehova, “Farao akandimvera bwanji, pakuti ine sinditha kuyankhula bwino?” Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona ine ndakuyika kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mʼbale wako Aaroni adzakhala mneneri wako. Iwe ukanene zonse zimene ndakulamulirazi, ndipo Aaroni mʼbale wako ndiye akaziyankhule kwa Farao kuti atulutse ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Koma ndidzawumitsa mtima wa Farao, ndipo ngakhale nditachulukitsa zizindikiro zozizwitsa ndi zodabwitsa mu Igupto, iyeyo sadzakumverani. Choncho ndidzakantha Igupto, ndipo ndi ntchito zachiweruzo ndidzatulutsa magulu anga, anthu anga Aisraeli kuwachotsa mʼdziko la Igupto. Ndipo Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, ndikadzatambasula dzanja langa kukantha Igupto ndi kutulutsa Aisraeli mʼdzikomo.” Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova anawalamulira. Mose anali ndi zaka 80, ndipo Aaroni anali ndi zaka 83 pamene anakayankhula kwa Farao. Ndodo ya Aaroni Isanduka Njoka Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Ngati Farao adzati kwa inu, ‘Chitani chozizwitsa,’ iwe Mose udzati kwa Aaroni, ‘Tenga ndodo yako ndipo uyiponye pamaso pa Farao,’ ndipo idzasanduka njoka.” Kotero Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kuchita monga momwe Yehova anawalamulira. Aaroni anaponya ndodo yake pansi patsogolo pa Farao ndi nduna zake ndipo inasanduka njoka. Naye Farao anayitanitsa anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo nawonso amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Aliyense wa iwo anaponya ndodo yake pansi ndipo inasanduka njoka. Koma ndodo ya Aaroni inameza ndodo zawo. Koma mtima wa Farao unawuma ndipo sanawamvere monga momwe Yehova ananenera. Mliri wa Magazi Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Farao ndi wowuma mtima. Akukana kulola anthu anga kuti apite. Upite kwa Farao mmawa pamene azidzapita ku madzi. Ukamudikire mʼmbali mwa Nailo kuti ukakumane naye ndipo unyamule ndodo imene inasanduka njoka ija mʼdzanja lako. Ndipo ukamuwuze Farao kuti, ‘Yehova, Mulungu wa Ahebri wandituma kuti ndikuwuzeni kuti: Lolani anthu anga apite kuti akandipembedze mʼchipululu. Koma mpaka tsopano inu simunandimvere. Izi ndi zimene Yehova akunena: Ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa ndidzamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi adzasanduka magazi. Ndikadzachita ichi udzadziwa kuti Ine ndine Yehova: Nsomba za mu Nailo zidzafa, mtsinje udzanunkha ndipo Aigupto sadzatha kumwa madzi ake.’ ” Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Tenga ndodo yako uyilozetse ku madzi a mu Igupto pa mitsinje, pa ngalande, pa zithaphwi ndi pa madambo, ndipo onse adzasanduka magazi.’ Mʼdziko lonse la Igupto mudzakhala magazi, ngakhale mʼzotungira madzi zopangidwa ndi mitengo ndi miyala.” Mose ndi Aaroni anachita monga momwe Yehova analamulira. Anakweza ndodo yake pamaso pa Farao ndi akuluakulu ake ndipo anamenya madzi a mu Nailo, ndipo madzi onse anasanduka magazi. Nsomba za mu Nailo zinafa ndipo mtsinje unanunkha kwambiri kotero kuti Aigupto sanathe kumwa madzi ake. Magazi anali ponseponse mu Igupto. Koma amatsenga a Chiigupto anachita zinthu zomwezo mwa matsenga awo. Choncho Farao anawumabe mtima, ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananeneratu. Mʼmalo mwake iye anatembenuka ndi kupita ku nyumba yake yaufumu ndipo zimenezi sanazilabadire. Anthu onse a ku Igupto anayamba kukumba mʼmbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sanathe kumwa madzi a mu mtsinjemo. Mliri wa Achule Panapita masiku asanu ndi awiri Yehova atamenya madzi a mu mtsinje wa Nailo. Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Ukamuwuze Farao kuti, Lolani anthu anga kuti apite, akandipembedze. Ndipo ngati simulola kuti apite Ine ndidzalanga dziko lonse la Igupto polidzaza ndi achule. Mtsinje wa Nailo udzadzaza ndi achule. Achulewo adzatuluka ndi kukalowa mʼnyumba yaufumu, ku chipinda chogona ndi pa bedi lako, mʼnyumba za nduna zako ndi pa anthu ako ndi mophikira buledi ndiponso mopangira bulediyo. Achulewo adzakulumphira iwe ndi anthu ako ndiponso nduna zako.” Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti, ‘Loza ndodo yako ku mitsinje, ku ngalande ndi ku zithaphwi ndipo pakhale achule pa dziko lonse la Igupto.’ ” Kotero Aaroni analoza dzanja lake pa madzi a ku Igupto, ndipo achule anatuluka nadzaza dziko lonse la Igupto. Koma amatsenga anachita zinthu zomwezo mʼmatsenga awo. Iwonso anatulutsa achule mʼdziko lonse la Igupto. Kenaka, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Pemphera kwa Yehova kuti achulewa achoke kwa ine ndi anthu anga, ndipo ine ndidzalola kuti anthu anu apite kukapereka nsembe kwa Yehova.” Mose anati kwa Farao, “Inu mungonditchulira nthawi imene mukufuna kuti ndikupempherereni, nduna zanu pamodzi ndi anthu anu kuti achule achoke mʼnyumba zanu ndi kuti atsale okhawo ali mu mtsinje wa Nailo.” Farao anati, “Mawa.” Mose anamuyankha kuti, “Chabwino zidzakhala monga mwaneneramu, kuti mudzadziwe kuti palibe wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu. Achule adzachoka mʼnyumba yanu, mʼnyumba za nduna zanu pamodzi ndi za anthu anu. Koma adzatsala mu mtsinje wa Nailo basi.” Mose ndi Aaroni anachoka, ndipo Mose anapemphera kwa Yehova kuti achotse achule amene anatumiza kwa Farao. Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha. Achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anafa Aigupto anawunjika achulewo milumilu ndipo dziko linanunkha. Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera. Mliri wa Nsabwe Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aaroni kuti akweze ndodo yake ndi kumenya fumbi la pa nthaka, ndipo fumbilo lidzasanduka nsabwe pa dziko lonse la Igupto.” Iwo anachita momwemo, ndipo pamene Aaroni anakweza ndodo yake ndi kumenya fumbi, nsabwe zinafika pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Fumbi lonse la mʼdziko la Igupto linasanduka nsabwe. Koma amatsenga atayesa kupanga nsabwe mwa matsenga awo, analephera. Ndipo nsabwezo zinali pa munthu aliyense ndi pa ziweto zawo. Amatsenga anati kwa Farao, “Izi wachita ndi Mulungu.” Koma mtima wa Farao unali wowumabe ndipo sanamvere zonena za Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova ananenera. Mliri wa Ntchentche Zoluma Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mmawa, upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso pamene azidzapita ku madzi ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Lola anthu anga kuti apite akandipembedze. Koma ngati suwalola anthu anga kuti apite, Ine ndidzatumiza pa iwe ntchentche zoluma ndi pa nduna zako ndi anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Mʼnyumba za Aigupto mudzadzaza ntchentche zoluma. Ngakhale pa nthaka pamene akhalapo padzadzaza ndi ntchentche zoluma.’ ” “Koma pa tsikulo ndidzapatula dera la Goseni, kumene kumakhala anthu anga, motero kuti sikudzakhala ntchentche zoluma. Choncho iwe udzadziwa kuti Ine Yehova ndi amene ndikulamulira dziko lino. Ndidzasiyanitsa pakati pa anthu anga ndi anthu ako. Chizindikiro chozizwitsa ichi chidzachitika mawa.” Ndipo Yehova anachita zimenezi: Ntchentche zoluma zochuluka zinalowa mʼnyumba yaufumu ya Farao ndi nyumba za nduna zake. Choncho ntchentche zolumazi zinawononga dziko lonse la Igupto. Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu mʼdziko lomwe lino.” Koma Mose anati, “Sitingathe kutero pakuti nsembe zathu kwa Yehova Mulungu ndi zowayipira Aigupto. Ngati tipereke nsembe zowayipira Aigupto mʼmaso mwawo, adzatiponya miyala kuti tife. Ife tiyenera kuyenda ulendo wa masiku atatu kupita ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu monga anatilamulira.” Farao anati, “Ine ndikulolani kuti mupite ku chipululu kukapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma musapite kutali kwambiri. Tsopano ndipempherereni.” Mose anayankha kuti, “Ine ndikangochoka pano, ndikapemphera kwa Yehova ndipo mawa lomweli ntchentche zoluma zidzachoka kwa Farao, nduna zake pamodzi ndi anthu ake. Koma Farao, onetsetsani kuti musachitenso zachinyengo ndi kuwakaniza anthu kuti asakapereke nsembe kwa Yehova.” Choncho Mose anasiyana ndi Farao nakapemphera kwa Yehova. Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala. Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke. Mliri pa Ziweto Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao ndipo ukamuwuze kuti Yehova, Mulungu wa Ahebri akuti alole anthu anga apite kuti akandipembedze. Koma ngati ukana kuti apite ndi kupitiriza kuwaletsa, dzanja la Yehova lidzakantha ziweto zako zimene zili ku munda, pamodzi ndi akavalo, abulu, ngamira, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi ndi mliri woopsa kwambiri. Koma Yehova adzasiyanitsa pakati pa ziweto za Israeli ndi ziweto za Igupto, kotero kuti palibe chiweto nʼchimodzi chomwe cha Aisraeli chimene chidzafe.” Yehova anayika nthawi ndipo anati, “Yehova adzachita zimenezi mmawa mʼdziko muno.” Ndipo mmawa mwake Yehova anachitadi zimenezi. Ziweto zonse za Aigupto zinafa, koma palibe chiweto ndi chimodzi chomwe cha Aisraeli chomwe chinafa. Farao anatuma anthu kuti akafufuze ndipo anapeza kuti palibe chiweto chilichonse cha Aisraeli chomwe chinafa. Komabe mtima wake sunagonje ndipo iye sanalole kuti anthu apite. Mliri wa Zotupa Kenaka Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Tapani phulusa la pa moto lodzaza dzanja ndipo Mose aliwaze mmwamba pamaso pa Farao. Phulusalo lidzasanduka fumbi pa dziko lonse la Igupto. Tsono fumbilo lidzasanduka zithupsa zomaphulika nʼkukhala zilonda pa munthu aliyense ndi pa nyama zomwe mʼdziko lonse la Igupto.” Kotero anatenga phulusa la pa moto ndi kuyima pamaso pa Farao. Mose analiwaza mmwamba, ndipo panabuka zotupa zophulika zokha pa munthu aliyense ndi pa ziweto. Amatsenga sanathe kumuyandikira Mose chifukwa nawonso anali ndi zithupsa monga mmene analili Aigupto ena onse. Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo iye sanamvere Mose ndi Aaroni monga momwe Yehova anamuwuzira Mose. Mliri wa Mvula ya Matalala Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Mawa mmawa upite ukakumane ndi Farao maso ndi maso ndipo ukamuwuze kuti Yehova Mulungu wa Ahebri akuti ulole anthu anga apite kuti akandipembedze. Ngati suwalola, tsopano ndidzagwetsa miliri yanga yonse pa iwe ndi nduna zako ndiponso pa anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wina wofanana nane pa dziko lonse lapansi. Pakuti ndikanakhala nditatukula kale dzanja langa ndikupheratu iwe pamodzi ndi anthu ako onse pa dziko lapansi. Koma ndakuyika kukhala mfumu ndi cholinga choti ndionetse mphamvu zanga kwa iwe ndiponso kuti dzina langa litchuke pa dziko lonse lapansi. Komabe iwe ukudzitukumula pa anthu anga osawalola kuti atuluke. Nʼchifukwa chake mawa, nthawi ngati ino, ndidzagwetsa matalala amphamvu amene sanagwepo pa Igupto, kuyambira pachiyambi mpaka lero. Tsopano lamula kuti ziweto zanu zonse ndi zinthu zonse zomwe zili ku minda kuti zilowetsedwe mʼkhola, chifukwa matalala adzagwera munthu aliyense ndi chiweto chilichonse chimene sichidzalowetsedwa mʼkhola ndipo zimene zidzakhala zili ku munda zidzafa.” Nduna za Farao zinachita mantha ndi mawu a Yehova, ndipo zinalowetsa antchito awo ndi ziweto zawo mʼnyumba. Koma iwo amene ananyozera mawu a Yehova anasiya akapolo ndi ziweto zawo panja. Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Kweza dzanja lako kumwamba kuti matalala agwe pa dziko lonse la Igupto, pa munthu aliyense, pa ziweto ndi pa zonse zomera mʼminda ya Igupto.” Mose ataloza ndodo yake kumwamba, Yehova anatumiza mabingu ndi matalala ndi ziphaliwali zongʼanima pa nthaka. Kotero Yehova anagwetsa matalala pa dziko la Igupto. Matalala anagwa ndipo ziphaliwali zinangʼanima. Inali mphepo ya mkuntho yoopsa kwambiri imene sinakhaleponso mʼdziko lonse la Igupto chiyambire pamene Aigupto anakhala mtundu woyima pa okha. Matalala anawononga dziko lonse la Igupto, munthu aliyense pamodzi ndi ziweto. Matalala aja anawononga zomera zonse za mʼmunda ndi kukhadzula mtengo uliwonse. Ku malo kokhako kumene matalala sanafikeko ndi dera la Goseni kumene kunali Aisraeli. Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati kwa iwo, “Tsopano ndachimwa, Yehova ndi wolungama, ine ndi anthu anga ndife olakwa. Upemphere kwa Mulungu chifukwa mabingu ndi matalala atikwana. Ine ndidzakulolani kuti mupite. Simuyenera kukhalabe kuno.” Mose anayankha, “Ndikangotuluka mu mzinda muno, ine ndidzakweza manja anga kwa Yehova ndi kupemphera. Mabingu ndi matalalawa adzaleka ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova ndiye akulamulira dziko lapansi. Koma ine ndikudziwa kuti inu ndi nduna zanu simukuopabe Yehova Mulungu.” Thonje ndi barele zinawonongeka, popeza barele anali atakhwima ndi thonje linali ndi maluwa. Koma tirigu ndi mchewere sizinawonongeke chifukwa zimakhwima mochedwa. Mose anasiyana ndi Farao natuluka mu mzindawo. Iye anakweza manja ake kwa Yehova. Mabingu ndi matalala zinaleka, ndipo mvula inalekeratu kugwa mʼdzikolo. Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zaleka, anachimwanso. Iye ndi nduna zake anawumitsanso mitima yawo. Choncho Farao sanalole kuti Aisraeli apite monga momwe Yehova anamuwuzira Mose. Mliri wa Dzombe Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa Farao, pakuti Ine ndawumitsa mtima wake ndi mitima ya nduna zake kuti ndichite zizindikiro zozizwitsa pakati pawo kuti inu mudzawuze ana ndi zidzukulu zanu za mmene ndinawakhawulitsira Aigupto ndi zizindikiro zozizwitsa zimene ndinachita pakati pawo ndiponso kuti inu mudziwe kuti ine ndine Yehova.” Ndipo Mose ndi Aaroni anapita kwa Farao ndi kukanena kuti, “Yehova Mulungu wa Ahebri, akuti: ‘Kodi udzakanabe kudzichepetsa pamaso panga mpaka liti? Alole anthu anga apite kuti akandipembedze. Ngati ukana kuwalola, ndigwetsa dzombe mʼdziko lako lino mawa. Dzombeli lidzakuta nthaka yonse moti sidzaoneka konse. Lidzadya kalikonse kakangʼono kamene sikanawonongedwe ndi matalala aja, kuphatikizapo mitengo yonse imene ikumera mʼminda yanu. Dzombeli lidzadzaza nyumba zako ndi za nduna zako ndiponso za Aigupto onse, chinthu chimene ngakhale makolo anu kapena makolo awo sanachionepo kuyambira tsiku limene anakhala mʼdzikoli mpaka lero.’ ” Ndipo Mose ndi Aaroni anatembenuka ndi kumusiya Farao. Nduna za Farao zinamufunsa kuti, “Kodi munthu uyu adzativutitsa mpaka liti? Aloleni anthuwa apite, kuti akapembedze Yehova Mulungu wawo. Kodi simukuona kuti dziko la Igupto lawonongeka?” Choncho Mose ndi Aaroni anayitanidwanso kwa Farao ndipo anati, “Pitani kapembedzeni Yehova Mulungu wanu. Koma ndani amene adzapite?” Mose anayankha kuti, “Ife tidzapita tonse pamodzi; angʼonoangʼono ndi akuluakulu, ana athu aamuna ndi aakazi, ndiponso ziweto zathu ndi ngʼombe chifukwa tikakhala ndi chikondwerero cha kwa Yehova.” Farao anati, “Yehova akhale ndi inu ngati ndingakuloleni kupita pamodzi ndi akazi ndi ana anu! Zikuoneka kuti mwakonzeka kuchita choyipa. Ndakana! Amuna okha ndiwo apite ndi kukapembedza Yehova pakuti izi ndi zimene mwakhala mukupempha.” Kenaka Mose ndi Aaroni anathamangitsidwa pamaso pa Farao. Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Tambalitsa dzanja lako pa dziko la Igupto kuti dzombe lidze pa dziko la Igupto ndi kuwononga chilichonse chimene chikumera mʼminda ndi chilichonse chimene chinatsala pa nthawi ya matalala.” Kotero Mose anakweza ndodo yake pa dziko la Igupto, ndipo Yehova anawutsa mphepo ya kummawa imene inawomba pa dziko usana ndi usiku wonse. Mmene kumacha nʼkuti mphepoyo itabweretsa dzombe. Dzombelo linafika pa dziko lonse la Igupto ndi kukhala dera lililonse la dzikolo. Dzombe lambiri ngati limenelo silinakhaleponso nʼkale lonse ndipo silidzakhalapo ngakhale mʼtsogolo. Dzombelo linaphimba nthaka yonse mpaka kuoneka kuti bii. Linadya zonse zimene zinatsala nthawi ya matalala, zomera za mʼmunda ndi zipatso. Panalibe chobiriwira chilichonse chimene chinatsala pa mtengo kapena pa chomera chilichonse mʼdziko lonse la Igupto. Mwamsangamsanga, Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Ine ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso inu. Tsopano ndikhululukirenso tchimo langa kano konkha ndipo pempherani kwa Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wosakazawu.” Mose anachoka kwa Farao nakapemphera kwa Yehova. Ndipo Yehova anasintha mphepo ija kuti ikhale ya mphamvu yochokera ku madzulo, ndipo inanyamula dzombe lija nʼkulikankhira mʼNyanja Yofiira. Panalibe dzombe ndi limodzi lomwe limene linatsala mu Igupto. Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli apite. Mliri wa Mdima Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasulira dzanja lako kumwamba kuti kukhale mdima umene udzaphimba dziko lonse la Igupto, mdima wandiweyani.” Choncho Mose anakweza dzanja lake kumwamba ndipo mdima wandiweyani unaphimba dziko lonse la Igupto kwa masiku atatu. Palibe amene anatha kuona mnzake kapena kuchoka pa khomo pake kwa masiku atatu. Koma kumalo kumene kumakhala Aisraeli kunali kowala. Kenaka Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni nati, “Pitani kapembedzeni Yehova. Ngakhale akazi ndi ana anu apite pamodzi ndi inu. Koma musatenge ziweto zanu ndi ngʼombe zanu.” Koma Mose anati, “Ndiye inu mutipatse nsembe zopsereza zoti tikapereke kwa Yehova Mulungu wathu. Koma ayi, ife tipita ndi ziweto zathu. Palibe chiweto chilichonse chimene chitatsale kuno, popeza tikasankha komweko ziweto zokapembedzera Yehova. Sitingadziwe zimene tikagwiritse ntchito popembedza Yehova mpaka titakafika kumeneko.” Koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao ndipo sanafune kuwalola kuti apite. Farao anati kwa Mose, “Choka pamaso panga! Uwonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga! Tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.” Mose anayankha kuti, “Monga momwe mwaneneramu, Ine sindidzaonekeranso pamaso panu.” Mliri wa Imfa ya Ana Oyamba Kubadwa Tsopano Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzalanga Farao pamodzi ndi Aigupto onse ndi mliri umodzi wotsiriza. Zikadzachitika izi iye adzakulolani kuti mutuluke mʼdziko lino. Ndithu pamene azidzakutulutsani adzachita ngati akukuyingitsani. Awuze anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa mnansi wake ziwiya zasiliva ndi golide.” Tsono Yehova anachititsa Aigupto kuti akomere mtima Aisraeli. Komanso Mose anali wotchuka kwambiri mʼdziko la Igupto, pamaso pa nduna za Farao ndi anthu onse. Tsono Mose anawuza Farao kuti, “Pakati pa usiku, Yehova adzayenda pakati pa anthu a ku Igupto. Ndipo mwana aliyense wamwamuna wachisamba adzafa, kuyambira mwana wamwamuna wa Farao amene amakhala pa mpando waufumu, mpaka mwana wamwamuna wachisamba wa mdzakazi wake amene ali naye pa mtondo, komanso ana oyamba a ziweto. Kudzakhala kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, kumene sikunachitikepo ndipo sikudzachitikanso. Koma pakati pa Aisraeli, ngakhale galu sadzawuwa munthu aliyense kapena chiweto!” Kotero mudzadziwa kuti Yehova ndiye wasiyanitsa pakati pa Igupto ndi Israeli. Nduna zanu zonse zidzabwera kwa ine, kugwada pamaso panga ndi kunena kuti, “Pita iwe ndi anthu ako onse amene akukutsatirawa! Zimenezi zikadzachitika ine ndidzachoka.” Ndipo Mose anachoka kwa Farao atakwiya kwambiri. Yehova ananena kwa Mose kuti, “Farao adzakana kukumvera, kuti zodabwitsa zanga zichuluke mʼdziko la Igupto.” Mose ndi Aaroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao koma Yehova anawumitsa mtima wa Farao, ndipo sanalole kuti Aisraeli atuluke mʼdziko lake. Kukhazikitsidwa kwa Paska Yehova anayankhula kwa Mose ndi Aaroni mʼdziko la Igupto kuti, “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba wa chaka. Muliwuze khamu lonse la Israeli kuti pa tsiku la khumi la mwezi uno, munthu aliyense asankhire banja lake mwana wankhosa mmodzi. Banja lililonse litenge mwana wankhosa mmodzi. Ngati banja lili lochepa moti silingathe kudya nyama yonse ya nkhosa, ligawane ndi banja lomwe layandikana nalo nyumba. Mabanja adziwiretu chiwerengero cha anthu amene alipo pokonzekera zimenezi. Muwerengere kuchuluka kwa nyama imene anthu adzadye potengera mmene munthu mmodzi angadyere. Ziweto zimene musankhe ziyenera kukhala zazimuna za chaka chimodzi, zopanda chilema, ndipo zikhale nkhosa kapena mbuzi. Muzisunge mpaka tsiku la khumi ndi chinayi la mwezi, pamene gulu lonse la Aisraeli lidzaphe nyamazo madzulo. Ndipo adzatengeko magazi anyamazo ndi kuwaza pa mphuthu ziwiri za chitseko ndiponso pamwamba pa chitseko cha nyumba mmene adzadyeremo ana ankhosawo. Adzawotche nyamayo ndi kudya usiku womwewo, ndipo adzayidye ndi buledi wophikidwa popanda yisiti pamodzi ndi masamba wowawa. Musadzadye yayiwisi kapena yophika, koma mudzawotche yonse, mutu, miyendo ndi zamʼmimba. Musadzasiye nyama ina mpaka mmawa, ngati ina idzatsala mpaka mmawa, mudzayitenthe. Muzidzadya nyamayo mutavala chotere, pokonzekera ulendo: mudzazimangirire lamba mʼchiwuno, nsapato zanu kuphazi ndi ndodo yanu kumanja. Mudzadye mofulumira. Imeneyi ndi Paska ya Yehova. “Usiku umenewo Ine ndidzadutsa mʼdziko la Igupto ndipo ndidzapha chilichonse choyamba kubadwa kuyambira mwana wa munthu aliyense mpaka ana aziweto. Ndidzalanganso milungu yonse ya Igupto. Ine ndine Yehova. Magazi amene mudzawaze pa mphuthu za zitseko ndi pamwamba pa zitseko aja adzakhala ngati chizindikiro. Ine ndikadzaona magaziwo ndidzakudutsani, ndipo ndikadzamakantha anthu a Igupto, mliri wosakazawu sudzakukhudzani. “Ili ndi tsiku la chikumbutso. Tsiku limeneli muzidzachita chikondwerero, kupembedza Yehova. Mibado yonse imene ikubwera izidzakumbukira tsiku limeneli ngati lamulo lamuyaya ndi kuti pa tsikuli azidzachita chikondwerero cholemekeza Yehova. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti. Tsiku loyamba muzichotsa yisiti mʼnyumba zanu, ngati aliyense adzadya kanthu kalikonse kali ndi yisiti kuyambira tsiku loyamba mpaka tsiku lachisanu ndi chiwiri, munthu ameneyo adzayenera kuchotsedwa mʼgulu la Israeli. Pa tsiku loyamba muzichita msonkhano wopatulika, ndipo winanso uzikhala pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Musamagwire ntchito masiku onsewa, koma ntchito yokonza chakudya yokha kuti aliyense adye. Izi ndi zimene muzichita. “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti, chifukwa ndi pa tsiku limeneli ndinatulutsa magulu anu mʼdziko la Igupto. Muzikondwerera tsiku limeneli pa mibado yonse ngati lamulo lamuyaya. Mwezi woyamba muzidzadya buledi wopanda yisiti kuyambira madzulo tsiku la 14 la mweziwo mpaka tsiku la 21 mwezi womwewo. Yisiti asamapezeka mʼnyumba zanu kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo aliyense amene adya chakudya chimene muli yisiti, munthu ameneyo ayenera kuchotsedwa mʼgulu la Aisraeli, kaya iyeyo ndi mlendo kapena mbadwa. Musadye chilichonse chokhala ndi yisiti. Kulikonse kumene mukukhala, muyenera kudya buledi wopanda yisiti.” Ndipo Mose anasonkhanitsa akuluakulu onse a Israeli nati, “Pitani msanga kukasankha nkhosa zokwanira pa mabanja anu, ndipo muziphe ngati Paska. Mutengenso nthambi ya chitsamba cha hisope, muchiviyike mʼmagazi amene mwawayika mʼbeseni ndipo muwaze ena mwa magaziwo pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko. Palibe aliyense wa inu amene adzatuluke mʼnyumba yake mpaka mmawa. Pamene Yehova adzadutsa mʼdziko kudzakantha Aigupto, nʼkuona magazi pamwamba ndi mʼmbali mwa mphuthu za chitseko, Iye adzadutsa khomo limenelo ndipo sadzalola woonongayo kuti alowe mʼnyumba zanu kuti akukantheni. “Muzimvera malamulo amenewa kwa muyaya, inu ndi zidzukulu zanu. Mukakalowa mʼdziko limene Yehova adzakupatseni monga analonjeza, mukasunge mwambo umenewu. Ndipo ana anu akakakufunsani kuti, ‘Mwambo umenewu ukutanthauza chiyani?’ Inu mukawawuze kuti, ‘Ndi nsembe ya Paska ya Yehova, popeza pamene ankakantha nyumba za Aigupto anasiya nyumba zathu.’ ” Kenaka anthu anawerama napembedza. Aisraeli anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni. Pakati pa usiku Yehova anakantha ana onse oyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira woyamba kubadwa wa Farao, amene amakhala pa mpando waufumu wa Faraoyo, mpaka mwana woyamba kubadwa wa munthu amene anali mʼdzenje, pamodzinso ndi ana oyamba kubadwa a ziweto zawo. Farao ndi nduna zake zonse ndiponso Aigupto onse anadzuka pakati pa usiku, ndipo kunali kulira kwakukulu mʼdziko lonse la Igupto, pakuti panalibe nyumba imene munalibe munthu wakufa. Kutuluka kwa Aisraeli Pakati pa usiku Farao anayitanitsa Mose ndi Aaroni ndipo anati, “Nyamukani! Asiyeni anthu anga, inu ndi Aisraeli! Pitani, kapembedzeni Yehova monga munapempha. Tengani ziweto ndi ngʼombe zanu ndipo pitani kapembedzeni Mulungu wanu monga munanenera kuti ine ndidalitsike.” Aigupto anawawumiriza anthuwo kuti atuluke mofulumira ndi kusiya dziko lawo. Iwo anati, “Ngati sitiwalola kutero, tonse tidzafa.” Motero anthuwo ananyamula ufa wawo wopangira buledi asanathiremo yisiti ndipo anasenza pa mapewa awo pamodzi ndi zokandiramo buledi atazikulunga mu nsalu. Aisraeli anachita monga anawawuzira Mose kuti apemphe kwa Aigupto zozikongoletsera zasiliva ndi zagolide ndi zovala. Yehova anafewetsa mtima Aigupto kuti akomere mtima Aisraeliwo ndipo anawapatsa zimene anawapempha. Motero Aisraeli anawalanda zinthu Aigupto. Aisraeli anayenda ulendo kuchokera ku Ramesesi mpaka kukafika ku Sukoti. Anthu aamuna oyenda pansi analipo 600,000 osawerengera akazi ndi ana. Anthu enanso ambiri anapita nawo, kuphatikizanso gulu lalikulu la ziweto, mbuzi, nkhosa pamodzi ndi ngʼombe. Iwo anapanga buledi wopanda yisiti ndi ufa umene anachoka nawo ku Igupto. Ufawo unalibe yisiti chifukwa anachita kuthamangitsidwa ku Igupto ndipo analibe nthawi yokonzera chakudya chawo. Ndipo Aisraeli anakhala ku Igupto kwa zaka 430. Pa tsiku lomwelo limene anakwanitsa zaka 430, magulu onse a Yehova anatuluka mʼdziko la Igupto. Usiku wonse Yehova anachezera kutulutsa ana a Israeli mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake pa tsiku limeneli Aisraeli onse azichezera usiku wonse kulemekeza Mulungu kamba ka mibado yonse ya mʼtsogolo. Lamulo la Paska Yehova anati kwa Mose ndi Aaroni, “Malamulo a Paska ndi awa: “Mlendo asadye Paska. Kapolo aliyense amene munagula angadye ngati atayamba wachita mdulidwe. Koma amene mukukhala naye kwa kanthawi kapena waganyu asadye Paska. “Muzidyera Paska mʼnyumba imodzi. Musatulutse nyama iliyonse kunja kwa nyumba. Musaswe mafupa aliwonse. Gulu lonse la Israeli lizichita mwambo wachikondwererochi. “Ngati mlendo wokhala pakati panu angafune kuchita nawo mwambo wa chikondwerero cha Paska, cha Yehovachi, amuna onse a mʼnyumba mwake ayenera kuchita mdulidwe. Akatero muzimutenga ngati mbadwa pakati panu. Koma aliyense wosachita mdulidwe asadye Paska. Lamulo limeneli likhudza mbadwa ngakhalenso alendo wochita mdulidwe wokhala pakati panu. “Aisraeli onse anachita monga momwe Yehova analamulira Mose ndi Aaroni. Ndipo tsiku lomwelo Yehova anatulutsa gulu lonse la ana a Israeli mʼdziko la Igupto.” Mwambo Wopatula Ana Oyamba Kubadwa Yehova anati kwa Mose, “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.” Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti. Pa tsiku la lero mwezi uno wa Abibu, mukutuluka mʼdziko la Igupto. Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanaani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi, dziko loyenda mkaka ndi uchi, muzikachita mwambo uwu mwezi uno. Muzidzadya buledi wopanda yisiti kwa masiku asanu ndi awiri ndipo tsiku lachisanu ndi chiwirilo muzichita chikondwerero cha Yehova. Mudye buledi wopanda yisiti masiku asanu ndi awiri. Pasapezeke chinthu chilichonse chokhala ndi yisiti pakati panu, kapena paliponse mʼdziko lanu. Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’ Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu. Muzichita mwambo uwu pa nthawi yake chaka ndi chaka. “Yehova akadzakulowetsani ndi kukupatsani dziko la Kanaani monga analonjezera kwa inu ndi makolo anu, muzikapereka kwa Ambuye ana onse oyamba kubadwa. Ziweto zonse zazimuna zoyamba kubadwa ndi za Ambuye. Koma mwana woyamba kubadwa wa bulu muzikamuwombola ndi mwana wankhosa, koma ngati simukamuwombola, muzikamuthyola khosi. Mwana wamwamuna woyamba kubadwa muzikamuwombola. “Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu. Farao atakanitsitsa kuti asatitulutse, Yehova anapha aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Igupto, kuyambira ana a anthu ndi ziweto zomwe. Nʼchifukwa chake ine ndimapereka nsembe kwa Yehova, chachimuna chilichonse choyamba kubadwa ndipo mwana wamwamuna woyamba kubadwa ndimamuwombola.’ Ndipo chidzakhala kwa inu ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi pamphumi panu kuonetsa kuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.” Kuwoloka Nyanja Farao atalola anthu aja kuti atuluke, Mulungu sanawadzeretse njira yodutsa dziko la Afilisti, ngakhale kuti inali yachidule popeza Mulungu anati, “Ngati anthuwa atadzakumana ndi nkhondo angadzakhumudwe ndi kubwerera ku Igupto.” Choncho Mulungu anawadzeretsa anthuwo njira yozungulira ya mʼchipululu kulowera ku Nyanja Yofiira. Komabe Aisraeli anatuluka mʼdziko la Igupto atakonzekera nkhondo. Mose ananyamula mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe anawalumbiritsa ana a Israeli. Iye anawawuza kuti, “Mulungu adzabwera ndithu kudzakuthandizani, ndipo mudzanyamule mafupa anga pochoka ku malo ano.” Atachoka ku Sukoti anakagona ku Etamu mʼmphepete mwa chipululu. Nthawi yamasana Yehova amakhala patsogolo pa anthu kuwatsogolera njira ndi chipilala cha mtambo, ndipo usiku Yehova ankawatsogolera ndi chipilala cha moto, kuwawunikira njira kuti athe kuyenda masana ndi usiku. Usana, chipilala cha mtambo ndi usiku, chipilala cha moto zinali patsogolo kuwatsogolera anthu aja. Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Uza Aisraeli abwerere ndi kukagona pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja. Inu mumange zithando mʼmbali mwa nyanja moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. Farao adzaganiza kuti ‘Aisraeli asokonezeka nʼkumangozungulirazungulira mu dzikomo, chipululu chitawazinga.’ Ndidzawumitsa mtima wa Farao ndipo adzathamangira Aisraeliwo. Choncho ndikadzagonjetsa Farao ndi gulu lake lonse la nkhondo, Ine ndidzalemekezedwa.” Choncho Aisraeli aja anachita zimenezi. Farao, mfumu ya Igupto atamva kuti anthu aja athawa, iye pamodzi ndi nduna zake anasintha maganizo awo pa Israeli ndipo anati, “Ife tachita chiyani? Tawalola Aisraeli kuti apite ndi kuleka kutitumikira?” Choncho anakonzetsa galeta lake ndipo ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake. Iye anatenga magaleta 600 abwino kwambiri pamodzi ndi magaleta ena a dziko la Igupto. Anatenganso akuluakulu onse ankhondo. Yehova anawumitsa mtima wa Farao mfumu ya dziko la Igupto, kotero iye anawathamangira Aisraeli amene ankachoka mʼdzikomo mosavutika. Aigupto aja (kutanthauza akavalo ndi magaleta onse a Farao, okwera akavalowo pamodzi ndi gulu lonse la nkhondo) analondola Aisraeli aja ndipo anakawapeza pamalo pamene anamanga zithando paja, mʼmbali mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti, moyangʼanana ndi Baala-Zefoni. Tsono Farao anayandikira. Ndipo Aisraeli ataona kuti Aigupto akuwatsatira, anachita mantha aakulu ndipo anafuwula kwa Yehova. Iwo anafunsa Mose kuti, “Kodi nʼchifukwa chakuti kunalibe manda ku dziko la Igupto kuti iwe utibweretse muno mʼchipululu kuti tidzafe? Chimene watichitachi nʼchiyani, kutitulutsa mʼdziko la Igupto? Kodi sindizo zimene tinakuwuza mʼdziko la Igupto? Ife tinati, ‘Tileke titumikire Aigupto?’ Zikanatikomera kutumikira Aigupto kulekana ndi kufa mʼchipululu muno.” Mose anayankha anthu kuti, “Musachite mantha. Imani, ndipo muone chipulumutso chimene Yehova akuchitireni lero. Aigupto amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso. Yehova adzakumenyerani nkhondo. Inu mungokhala chete.” Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Chifukwa chiyani ukufuwulira kwa ine? Uwuze Aisraeli aziyenda. Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma. Ine ndidzawumitsa mitima ya Aigupto kotero kuti adzatsatirabe Aisraeli. Ndipo ine ndikadzagonjetsa Farao ndi asilikali ake onse ankhondo, okwera magaleta ndi akavalo, ndidzapeza ulemerero. Aigupto adzadziwa kuti Ine ndine Yehova akadzaona mmene ndipambanire Farao ndi magaleta ndi owayendetsa ake.” Ndipo mngelo wa Mulungu amene amayenda patsogolo pa gulu lankhondo la Israeli anachoka ndi kupita kumbuyo kwawo. Chipilala cha mtambo chinasunthanso kuchoka kutsogolo ndi kupita kumbuyo kwawo. Choncho mtambowo unakhala pakati pa asilikali ankhondo a dziko la Igupto ndi a dziko la Israeli. Choncho panali mdima motero kuti magulu awiri ankhondowa sanathe kuyandikizana usiku wonse. Kenaka Mose anatambalitsa dzanja lake pa nyanja, ndipo Yehova pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu ya kummawa imene inawomba usiku wonse anabweza madzi ndi kuwumitsa nyanja ija. Choncho nyanja ija inagawanika. Ndipo Aisraeli anawoloka pakati pa nyanja powuma, madzi atasanduka khoma kumanja ndi kumanzere kwawo. Aigupto onse, Farao, ndi onse okwera pa magaleta ndi akavalo anawalondola ndipo analowa mʼmadzi. Kutatsala pangʼono kucha, Yehova ali mu chipilala chamoto ndi chamtambo, anayangʼana asilikali ankhondo a Igupto ndipo anabweretsa chisokonezo pakati pawo. Yehova anamanga matayala a magaleta kotero kuti ankavutika kuyenda. Ndipo Aigupto anati, “Tiyeni tiwathawe Aisraeli! Yehova akuwamenyera nkhondo kulimbana nafe.” Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tambasula dzanja lako pa nyanja kuti madzi amize Aigupto ndi magaleta awo ndi okwera pa akavalo.” Mose anatambasula dzanja lake pa nyanja, ndipo mmene kumacha nyanja inabwerera mʼmalo mwake. Aigupto pothawa anakumana nayo, ndipo Yehova anawakokera mʼnyanja momwemo. Madzi anabwerera ndi kumiza magaleta ndi okwera akavalo, asilikali ankhondo onse amene anatsatira Aisraeli mʼnyanja, palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka. Koma Aisraeli aja anawoloka nyanja pansi pali powuma, madzi atachita khoma kumanja ndi kumanzere kwawo. Tsiku limeneli Yehova anapulumutsa Israeli mʼmanja mwa Aigupto ndipo Israeli anaona Aigupto ali lambalamba mʼmbali mwa nyanja atafa Choncho Aisraeli anaona dzanja lamphamvu la Yehova limene linagonjetsa Aigupto aja, ndipo iwo anaopa Yehova ndi kumukhulupirira pamodzi ndi mtumiki wake Mose. Nyimbo ya Mose ndi Miriamu Ndipo Mose ndi Aisraeli anayimbira Yehova nyimbo iyi: “Ine ndidzayimbira Yehova pakuti wakwezeka mʼchigonjetso. Kavalo ndi wokwera wake, Iye wawaponya mʼnyanja. Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga; ndiye chipulumutso changa. Iye ndiye Mulungu wanga, ndipo ndidzamutamanda, Mulungu wa makolo anga, ine ndidzamukweza. Yehova ndi wankhondo; Yehova ndilo dzina lake. Magaleta a Farao ndi asilikali ake ankhondo Iye wawaponya mʼnyanja. Akatswiri ankhondo amphamvu a Farao amizidwa mʼNyanja Yofiira. Nyanja yakuya inawaphimba; Iwo anamira pansi ngati mwala.” Yehova, dzanja lanu lamanja ndi laulemerero chifukwa cha mphamvu zake. Ndithu Yehova, dzanja lanu lamanja linaphwanya mdani. Ndi ulemerero wanu waukulu, munagonjetsa okutsutsani. Inu munatumiza mkwiyo wanu waukulu; ndipo unawapsereza ngati udzu. Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu madzi anawunjikana pamodzi. Nyanja yakuya ija inasanduka madzi owuma gwaa kufika pansi. Mdaniyo anati, “Ine ndidzawalondola, ndipo ndidzawagwira. Ndidzagawa chuma chawo; ndiye chokhumba changa chidzakwaniritsidwa. Ine ndidzasolola lupanga langa, ndi mkono wanga ndidzawawononga.” Koma Inu munawuzira mphepo yanu, ndipo nyanja inawaphimba. Iwo anamira ngati chitsulo mʼmadzi amphamvu. Ndithu Yehova, pakati pa milungu, ndani afanana nanu? Inu amene muli woyera, ndiponso wotamandika wolemekezeka, chifukwa cha ntchito zanu, zazikulu ndi zodabwitsa? Munatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko linawameza. Ndi chikondi chanu chosasinthika mudzatsogolera anthu amene munawawombola. Ndi mphamvu zanu munawatsogolera ku malo anu woyera. Anthu amitundu ina anamva za mbiriyi ndipo ananjenjemera ndi mantha, mantha woopsa agwira anthu a dziko la Filisiti. Tsopano mafumu a ku Edomu agwidwa ndi mantha aakulu, otsogolera a dziko la Mowabu akunjenjemera ndi mantha, ndipo anthu a ku Kanaani asungunuka ndi mantha. Onse agwidwa ndi mantha woopsa. Popeza anaona mphamvu zanu zazikulu, iwo ayima chilili ngati mwala mpaka anthu anu, Inu Yehova atadutsa; inde mpaka atadutsa anthu amene munawagula. Inu mudzawalowetsa ndi kuwakhazikitsa pa phiri lanu. Pa malo pamene Inu Yehova munawapanga kuti muzikhalapo; malo wopatulika amene Inu Ambuye munawakonza ndi manja anu. “Yehova adzalamula mpaka muyaya.” Akavalo a Farao, magaleta ndi oyendetsa akavalo atalowa mʼnyanja, Yehova anawabwezera madziwo mʼnyanja ndi kuwamiza, koma Aisraeli anawoloka nyanjayo powuma. Ndipo Miriamu mneneri wamkazi, mlongo wa Aaroni anatenga zoyimbira ndipo akazi onse anamutsatira pambuyo, akuyimba ndi zoyimbira ndi kuvina. Miriamu anawayimbira nyimbo iyi: “Imbirani Yehova, chifukwa iye wapambana. Kavalo ndi wokwerapo wake Iye wawamiza mʼnyanja.” Madzi a ku Mara ndi Elimu Ndipo Mose anatsogolera Israeli kuchoka ku nyanja yofiira ndi kupita ku chipululu cha Suri. Anayenda mʼchipululu masiku atatu wosapeza madzi. Ndipo anafika ku Mara. Koma sanathe kumwa madzi akumeneko chifukwa anali owawa. (Ndi chifukwa chake malowo amatchedwa Mara). Tsono anthu aja anadandaulira Mose ndi kumufunsa kuti, “Kodi tikumwa chiyani?” Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anamuonetsa kamtengo. Iye anakaponya mʼmadzimo ndipo madzi anakhala abwino. Kumeneko Yehova anawayikira lamulo ndi maweruziro. Kumenekonso Yehova anawayesa. Yehova anati, “Ngati inu mudzamvetsa bwino mawu anga, kuchita zolungama, kumvera malamulo anga ndi kusamalitsa zimene ndikukuwuzani ndiye kuti Ine sindidzayika pa inu matenda amene ndinayika pa anthu a ku Igupto popeza ndine Yehova amene ndimakuchiritsani.” Kenaka anafika ku Elimu, kumene kunali akasupe khumi ndi awiri ndi mitengo ya migwalangwa makumi asanu ndi awiri, ndipo anamanga misasa yawo kumeneko pafupi ndi madzi. Mana ndi Zinziri Pambuyo pake gulu lonse la Aisraeli linachoka ku Elimu, ndipo pa tsiku la khumi ndi chisanu mwezi wachiwiri chichokere mʼdziko la Igupto, anafika ku chipululu cha Sini chimene chinali pakati pa Elimu ndi Sinai. Mʼchipululumo gulu lonse linadandaulira Mose ndi Aaroni kuti, “Kukanakhala bwino Yehova akanatiphera mʼdziko la Igupto! Kumeneko timadya nyama ndi buledi mpaka kukhuta, koma inu mwabwera nafe ku chipululu kudzapha mpingo wonsewu ndi njala!” Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzakupatsani buledi wogwa kuchokera kumwamba ngati mvula. Anthu azituluka tsiku lililonse kukatola buledi wokwanira tsiku limenelo. Ine ndidzawayesa mʼnjira imeneyi kuti ndione ngati adzatsatira malangizo anga. Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi, pamene azidzakonza buledi amene abwera naye, adzapeza kuti ndi wokwanira masiku awiri.” Kotero Mose ndi Aaroni anati kwa Aisraeli onse, “Nthawi yamadzulo inu mudzadziwa kuti ndi Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto. Ndipo mmawa mudzaona ulemerero wa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu. Kodi ife ndi yani kuti muzitidandaulira?” Mose anati, “Yehova adzakupatsani nyama madzulo aliwonse ndi buledi mmawa uliwonse kuti mukhute chifukwa Iye wamva madandawulo anu. Nanga ife ndi yani? Kudandaula kwanu simudandaulira ife, koma Yehova.” Kenaka Mose anawuza Aaroni kuti, “Uza gulu lonse la Aisraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova pakuti wamva kudandaula kwanu.’ ” Pamene Aaroni amayankhula ndi gulu lonse la Aisraeli, iwo anayangʼana ku chipululu, ndipo ulemerero wa Yehova umaoneka mu mtambo. Yehova anati kwa Mose, “Ine ndamva kudandaula kwa Aisraeli. Awuze kuti, ‘Madzulo mudzadya nyama ndipo mmawa mudzakhuta buledi. Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ” Madzulo amenewo panatuluka zinziri zimene zinali ponseponse pa misasa yawo, ndipo mmawa panali mame kuzungulira misasa yawo. Mamewo atachoka, pa nthaka mʼchipululumo panaoneka tinthu tina topyapyala komanso totuwa ngati chipale. Aisraeli atationa anafunsana wina ndi mnzake nati, “Kodi timeneti nʼchiyani?” Popeza sanatidziwe. Mose anawawuza kuti, “Uyu ndi buledi amene Yehova wakupatsani kuti mudye. Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole zomukwanira kudya, malita awiri pa munthu mmodzi molingana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mu tenti yanu.’ ” Aisraeli anachita zonse anawawuza. Ena anatola zambiri ena zochepa. Ndipo iwo atayeza ndi muyeso wa malita awiri, iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere. Aliyense anatola zomukwanira kudya. Ndipo Mose anawawuza kuti, “Wina aliyense asasunge mpaka mmawa.” Komabe ena sanamvere Mose, anasungako mpaka mmawa. Koma mmawa mwake tonse tinali mphutsi zokhazokha. Kotero Mose anawapsera mtima. Mmawa uliwonse aliyense amatola zimene amazifuna, ndipo dzuwa likatentha zimasungunuka. Tsiku lachisanu ndi chimodzi anatuta malita anayi munthu aliyense, ndipo atsogoleri a mpingo wonse anabwera kudzawuza Mose za zimenezi. Iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova analamula, ‘Mawa ndi tsiku lopumula, Sabata Loyera la Yehova, choncho wotchani ndi kuphika zimene mukufuna. Sungani zotsala mpaka mmawa.’ ” Choncho anasunga mpaka mmawa monga Mose anawalamulira, ndipo sananunkhe kapena kuchita mphutsi. Mose anati, “Idyani lero chifukwa lero ndi Sabata la Yehova. Lero simukapeza chilichonse kunjaku. Muzitola chakudya masiku asanu ndi limodzi koma tsiku la chisanu ndi chiwiri ndi la Sabata, simukapeza chilichonse kunjaku.” Komabe anthu ena anapita kuti akatole chakudya tsiku lachisanu ndi chiwiri, koma sanapeze kanthu. Ndipo Yehova anafunsa Mose nati, “Kodi inu muzipitirira kukana kusunga malamulo ndi malangizo anga mpaka liti? Taonani, popeza Yehova wakupatsani Sabata nʼchifukwa chake tsiku lachisanu ndi chimodzi amakupatsani chakudya cha masiku awiri. Aliyense azikhala pamene ali pa tsiku lachisanu ndi chiwiri, pasapezeke wotuluka kunja.” Kotero anthu anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri. Aisraeli anatchula chakudyacho Mana. Chakudyacho chinkaoneka ngati mbewu zamapira, zoyera. Ndipo chinkakoma ngati chothira uchi. Mose anati, “Chimene Yehova walamula ndi ichi: ‘Tengani muyeso wa malita awiri a mana ndi kusungira mibado imene ikubwera, kuti iwo adzaone chakudya chimene Ine ndinakupatsani kuti mudye mʼchipululu pamene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ” Choncho Mose anati kwa Aaroni, “Tenga mtsuko ndipo uyikemo malita awiri a mana. Ndipo uyike manawo pamaso pa Yehova kusungira mibado imene ikubwera.” Monga momwe Yehova analamulira Mose, Aaroni anayika mtsuko uja pafupi ndi bokosi la Chipangano kuti manawo asungike. Aisraeli anadya mana zaka 40, mpaka pamene anafika ku dziko kumene amati akakhazikeko. Iwo anadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a Kanaani. (Malita awiri amafanana ndi gawo lakhumi la efa). Madzi Otuluka Mʼthanthwe Gulu lonse la Aisraeli linachoka ku chipululu cha Sini, ndi kumayenda malo ndi malo monga momwe anawalamulira Yehova. Iwo anamanga misasa yawo ku Refidimu koma kunalibe madzi woti anthu onse ndi kumwa. Kotero iwo anakangana ndi Mose nati, “Tipatse madzi akumwa.” Mose anayankha kuti, “Chifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Chifukwa chiyani mukumuyesa Yehova?” Koma anthu anali ndi ludzu pamenepo ndipo anangʼungʼudza pamaso pa Mose namufunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani unatitulutsa mʼdziko la Igupto kuti ife, ana athu pamodzi ndi ziweto zathu tife ndi ludzu?” Ndipo Mose anapemphera kwa Yehova, “Kodi ndichite chiyani ndi anthu awa? Iwo atsala pangʼono kundigenda ndi miyala.” Yehova anati kwa Mose, “Pita patsogolo pa anthuwo. Tenga ndodo imene unamenyera nyanja ya Nailo pamodzi ndi akuluakulu ena a Israeli ndi kunyamuka. Ine ndidzayima patsogolo pako pafupi ndi thanthwe la ku Horebu. Ukamenye thanthwelo, madzi adzatuluka kuti anthu amwe.” Motero Mose anachita zimenezi pamaso pa akuluakulu a Israeli. Ndipo iye anatcha malowo Masa ndi Meriba chifukwa Aisraeli anakangana ndi kuyesa Yehova ponena kuti, “Kodi pakati pathu pali Yehova kapena palibe?” Aisraeli Agonjetsa Aamaleki Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli. Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.” Ndipo Yoswa anachitadi monga Mose anamulamulira. Iye anapita kukamenyana ndi Aamaleki ndipo Mose, Aaroni ndi Huri anapita pamwamba pa phiri. Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana. Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa. Kotero Yoswa anagonjetsa asilikali ankhondo a Amaleki ndi lupanga. Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.” Mose anamanga guwa lansembe ndipo analitcha Yehova Chipambano Changa (Yehova Nisi). Ndipo anati, “Kwezani mbendera ya Yehova. Yehova adzachitabe nkhondo ndi mibado yonse ya Aamaleki.” Yetero Abwera Kudzaona Mose Yetero wansembe wa ku Midiyani amenenso anali mpongozi wa Mose, anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake a Aisraeli ndi mmene Yehova anawatulutsira mʼdziko la Igupto. Mose atamubweza Zipora, mkazi wake, Yetero, mpongozi wake anamulandira mwana wake wamkaziyo pamodzi ndi ana ake aamuna awiri. Mose anamupatsa mwana wachisamba dzina loti Geresomu popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” Ndipo mwana wake wachiwiri anamupatsa dzina loti Eliezara, pakuti anati, “Mulungu wa makolo anga anali thandizo langa. Iye anandipulumutsa ku lupanga la Farao.” Yetero, mpongozi wa Mose pamodzi ndi ana a Mose aamuna awiri ndi mkazi wake anabwera kwa Mose ku chipululu pa phiri la Mulungu kumene Mose anamanga misasa. Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.” Kotero Mose anatuluka kukakumana ndi mpongozi wake ndipo anawerama ndi kupsompsona. Atalonjerana anakalowa mu tenti Mose anafotokozera mpongozi wake zonse zimene Yehova anamuchita Farao ndi Aigupto chifukwa cha Israeli komanso zowawa zonse anakumana nazo mʼnjira. Mose anafotokozanso momwe Yehova anawapulumutsira. Yetero anakondwa kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisraeli powapulumutsa mʼdzanja la Aigupto. Iye anati, “Alemekezeke Yehova amene wakupulumutsani mʼdzanja la Aigupto ndi Farao. Wapulumutsanso anthuwa mʼdzanja la Aigupto. Tsopano ndikudziwa kuti Yehova ndi wopambana milungu ina yonse, pakuti anachita izi kwa amene ananyoza Israeli.” Ndipo Yetero, mpongozi wa Mose anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Aaroni ndi akuluakulu onse a Israeli anabwera kudzadya chakudya pamodzi ndi mpongozi wa Mose pamaso pa Mulungu. Mmawa mwake, Mose anakhala pa mpando kuti aweruze milandu ya anthu. Anthu anayima momuzungulira kuyambira mmawa mpaka madzulo. Mpongozi wa Mose ataona zonse zimene iye amawachitira anthu anati, “Nʼchiyani chimene mukuwachitira anthuwa? Nʼchifukwa chiyani mulipo nokha woweruza, pamene anthu onsewa ayimirira kuyambira mmawa mpaka madzulo?” Mose anamuyankha kuti, “Chifukwa anthuwa anabwera kwa ine kudzafunsa zimene Mulungu akufuna. Ngati munthu akangana ndi mʼbale wake, onse awiri amabwera kwa ine, ndipo ine ndimawaweruza. Ndimawawuzanso malamulo a Mulungu ndi malangizo ake.” Mpongozi wa Mose anayankha kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Ntchitoyi ndi yayikulu kuposa mphamvu zanu. Inu simungathe kuyigwira nokha. Inu pamodzi ndi anthuwa amene amabwera kwa inu mudzatopa. Tsono tamverani ndikulangizeni, ndipo Mulungu akhale nanu. Inu muziwayimirira anthuwa pamaso pa Mulungu, ndipo mikangano yawo muzibwera nayo kwa Iye. Aphunzitseni mawu ndi malangizo a Mulungu. Aphunzitseni mmene ayenera kukhalira ndi zimene ayenera kuchita. Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi. Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana. Ngati mutsatira malangizowa monga mmene Mulungu wakulamulirani ndiye kuti simudzafowoka ndipo anthu onsewa adzapita kwawo mu mtendere.” Mose anamvera mpongozi wake ndi kuchita zonse zimene iye ananena. Iye anasankha amuna odziwa bwino ntchito zawo ndipo anawayika kuti akhale atsogoleri, oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 500, ena a anthu makumi asanu ndi ena a anthu khumi. Iwowa ankaweruza anthu nthawi zonse. Milandu yovuta ankabwera nayo kwa Mose, koma yosavuta ankayiweruza okha. Kenaka Mose analola kuti mpongozi wake, Yetero anyamuke kubwerera ku dziko la kwawo. Pa Phiri la Sinai Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto. Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo. Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti, ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. Tsopano, ngati mumveradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, mudzakhala chuma changa chapamtima pakati pa mitundu yonse. Ngakhale kuti dziko lonse lapansi ndi langa, inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.” Ndipo Mose anabwerera ndi kuyitanitsa akuluakulu. Atabwera anawafotokozera mawu amene Yehova anamulamulira kuti adzanene. Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova. Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena. Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa anthu onse ndi kuwayeretsa lero ndi mawa. Achape zovala zawo ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona. Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.” Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo. Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.” Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha. Ndipo Mose anatsogolera anthu kutuluka mʼmisasa kukakumana ndi Mulungu, ndipo anayima mʼmunsi mwa phiri. Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri. Liwu la lipenga linkakulirakulira. Tsono Mose anayankhula ndipo Yehova anamuyankha ndi mabingu. Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera, ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa. Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.” Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.” Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.” Ndipo Mose anatsika ndi kukawawuza anthuwo. Malamulo Khumi Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati: “Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo. “Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.” “Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga. “Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika. “Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera. “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa. “Usaphe. “Usachite chigololo. “Usabe. “Usapereke umboni womunamizira mnzako. “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.” Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.” Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.” Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu. Za Mafano ndi Maguwa Ansembe Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ” Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani. Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida. Musamakwere pa makwerero popita pa guwa langa lansembe kuti mungaonetse maliseche anu. “Uwawuze Aisraeli malamulo awa: Antchito a Chihebri “Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu. Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso. Ngati bwana wake amupatsa mkazi ndipo mkaziyo anabereka ana aamuna kapena aakazi, mkazi ndi anawo adzakhala a bwanayo ndipo mwamuna yekhayo ndiye adzamasulidwe. “Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, ‘Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’ mbuye wakeyo abwere naye kwa Yehova. Abwere naye pa chitseko kapena pa mphuthu zachitseko ndipo abowole khutu lake ndi chitsulo. Ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse. “Ngati munthu agulitsa mwana wake wamkazi kukhala mdzakazi, mwanayo asamasulidwe monga achitira ndi akapolo aamuna. Koma ngati mkaziyo sakukondweretsa bwana wake amene wamusankha kuti amukwatire, amulole kuti awomboledwe. Bwanayo alibe mphamvu zomugulitsa kwa anthu achilendo, chifukwa iyeyo waphwanya pangano lake lomukwatira iye. Ngati anamusankha kuti akhale mkazi wa mwana wake, ayenera kumusunga ngati mwana wake wamkazi. Ngati akwatira mkazi wina, asamumane woyambayo chakudya ngakhale chovala ndipo apiritirize kugona naye ngati mkazi wake. Koma ngati sangathe kumuchitira zonsezi, ndiye amuleke apite popanda kulipira kanthu. Munthu Akapwetekedwa “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, iyenso ayenera kuphedwa. Koma ngati sanachite dala, ndipo Mulungu analola kuti zichitike, iyeyo athawire ku malo kumene ndidzakupatsani. Koma ngati munthu akonza chiwembu ndi kupha mnzake mwadala, ameneyo muchotseni ngakhale ku guwa langa lansembe ndipo aphedwe. “Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa. “Munthu aliyense amene aba munthu mnzake, ndi kukamugulitsa, kapena kumangomusunga, ayenera kuphedwa. “Aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa. “Ngati anthu awiri akangana ndipo wina amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya koma wosamupha, womenyedwayo akadwala nagona pa bedi, kenaka nachira ndi kuyamba kuyenda ndi ndodo kutuluka kunja kwa nyumba yake, ndiye kuti womenya mnzakeyo sadzayimbidwa mlandu. Komabe adzayenera kulipira womenyedwayo chifukwa cha nthawi imene anagona pa bedi ija, ndiponso ayenera kumusala mpaka atachiritsitsa. “Ngati munthu amenya kapolo wake wamwamuna kapena mdzakazi ndi ndodo, kapolo uja ndikufa chifukwa cha kumenyedwako, munthuyo ayenera kulangidwa. Koma ngati kapolo uja akhala ndi moyo tsiku lonse kapena masiku awiri, ndiye kuti mbuye uja asalangidwe chifukwa kapolo ndi chuma chake. “Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza. Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, mkono kulipa mkono, phazi kulipa phazi. Kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, mkwingwirima kulipa mkwingwirima. “Ngati munthu amenya wantchito wake wa mwamuna kapena mdzakazi wake pa diso ndi kuliwononga, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a diso lake. Ndipo ngati agulula dzino la wantchito wamwamuna kapena mdzakazi, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a dzino lake. “Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu. Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso. Koma ngati wauzidwa kuti alipire, iye apereke zimene wauzidwazo kuti awombole moyo wake. Lamulo ili ligwirenso ntchito ngati ngʼombeyo yagunda mwana wamwamuna kapena wamkazi. Ngati ngʼombeyo yagunda kapolo wamwamuna kapena mdzakazi, mwini ngʼombeyo apereke masekeli makumi atatu a siliva kwa mwini kapoloyo, ndipo ngʼombeyo iponyedwe miyala. “Munthu akasiya dzenje lapululu kapena akakumba dzenje koma wosaphimbapo, ndipo ngʼombe kapena bulu nʼkugweramo, mwini dzenjelo amulipire mwini chiweto chakufacho koma iye atenge chiwetocho. “Ngati ngʼombe ya munthu wina ipha ngʼombe ya mnzake, ngʼombe yamoyo ija igulitsidwe ndipo anthu awiriwo agawane pakati ndalama yake. Achite chimodzimodzi ndi ngʼombe yakufa ija. Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.” Za Kuteteza Katundu “Ngati munthu aba ngʼombe kapena nkhosa ndi kuyipha kapena kuyigulitsa, iye abweze ngʼombe zisanu pa ngʼombe imodzi ndi nkhosa zinayi pa nkhosa imodzi. “Ngati mbala ipezeka ikuthyola nyumba ndipo imenyedwa nʼkufa, amene wapha mbalayo sanalakwe. Koma akayipha dzuwa litatuluka, woyiphayo ali ndi mlandu wakupha. “Mbala iyenera kubweza ndithu koma ngati ilibe kalikonse igulitsidwe, kulipira zomwe yabazo. “Ngati chiweto chobedwacho chipezeka chamoyo mʼmanja mwake, kaya ndi ngʼombe kapena bulu kapena nkhosa, mbalayo ibwezere ziweto ziwiri pa chiweto chobedwacho. “Ngati munthu alekerera ziweto zake kukalowa mʼmunda wa munthu wina kukadya mbewu zake, munthuyo amubwezere mwini mundawo mbewu zina zabwino kapena mpesa wina wabwino kwambiri. “Ngati munthu ayatsa moto, motowo ndikukafika mpaka ku munda ndi kuwotcha mulu wa tirigu kapena tirigu wosadula, kapena munda wonse, ndiye kuti munthu amene anayatsa motoyo alipire. “Ngati munthu asungitsidwa ndi mnzake ndalama kapena katundu, ndipo zinthu zija nʼkubedwa mʼnyumba mwake, wakubayo ngati agwidwa, ayenera kubwezera kawiri chobedwacho. Koma ngati mbalayo sipezeka, mwini nyumbayo ayenera kukaonekera ku bwalo lamilandu kuti akamve ngati anaba katundu wa mnzakeyo. Ngati pali kukangana kokhudza ngʼombe, bulu, nkhosa, zovala kapena kanthu kalikonse kotayika, ndipo mmodzi ndikunena kuti chinthucho nʼchake, awiriwo abwere nawo mlandu wawowo pamaso pa Mulungu ndipo amene mlandu umugomere adzayenera kumulipira mnzakeyo kawiri. “Ngati munthu wina anasungitsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa, kapena chiweto chilichonse ndipo chiweto chija nʼkufa kapena kupweteka kapena kutengedwa popanda wina kuona, ndiye kuti anthu awiriwo ayenera kulumbira pamaso pa Mulungu kuti asatenge chinthu cha mnzake. Zikatero mwini katundu uja avomereze zimenezi ndipo asabwezeredwe kanthu. Koma ngati chiwetocho chinabedwa, iye ayenera kubwezera mwini wakeyo. Ngati chinagwidwa ndi zirombo, iye ayenera kubweretsa zotsalira ngati umboni ndipo sadzalipira kanthu. “Ngati munthu abwereka chiweto cha mnzake ndipo chiweto chija nʼkuvulala kapena kufa chikanali ndi iyebe, wobwerekayo ayenera kulipira. Koma ngati mwini wakeyo ali ndi chiwetocho, wobwerekayo sadzalipira. Ngati anapereka ndalama pobwereka chiwetocho, ndalama anaperekazo zilowa mʼmalo mwa chiweto chakufacho. Malamulo a Kakhalidwe ka Anthu “Ngati munthu anyenga namwali wosadziwa mwamuna amene sanapalidwe ubwenzi ndi kugona naye, munthuyo ayenera kulipira malowolo ndipo adzakhala mkazi wake. Ngati abambo ake akanitsitsa kwamtuwagalu kumupereka kuti amukwatire, munthuyo aperekebe malowolo woyenera namwaliyo. “Musayilole mfiti yayikazi kuti ikhale ndi moyo. “Aliyense wogonana ndi chiweto ayenera kuphedwa. “Aliyense wopereka nsembe kwa mulungu wina osati Yehova awonongedwe. “Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto. “Musazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye. Ngati muwazunza ndipo iwo nʼkulirira kwa Ine, ndidzamva kulira kwawo. Ine ndidzakukwiyirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga. Akazi anu adzakhala amasiye ndiponso ana anu adzakhala wopanda abambo. “Ngati mukongoza ndalama kwa mʼbale wanu amene ndi mʼmphawi pakati panu, musadzamuchite monga zimene amachita wokongoza ndalama. Musadzamuyikire chiwongoladzanja. Mukatenga chovala cha mnzanu kuti chikhale chikole mumubwezere dzuwa lisanalowe chifukwa chovala chimene amadzifundira nacho nʼchomwecho. Nanga usiku adzafunda chiyani? Tsonotu ngati adzandilirira, Ine ndidzamva pakuti ndine wachifundo. “Musachite chipongwe Mulungu wanu kapena kutemberera mtsogoleri wa anthu anu. “Musachedwe kupereka kwa Ine zokolola zanu zochuluka ndi vinyo wanu wochuluka. “Mundipatse ana anu achisamba aamuna. Muchite chimodzimodzi ndi ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu. Mwana woyamba kubadwa azikhala ndi amayi ake masiku asanu ndi awiri. Koma pa tsiku lachisanu ndi chitatu mwanayo muzimupereka kwa Ine. “Inu mukhale anthu anga opatulika. Choncho musadye nyama ya chiweto chimene chaphedwa ndi zirombo. Nyamayo muwaponyere agalu.” Malamulo a Zachilungamo ndi Zachifundo “Usafalitse mbiri yabodza. Usathandize munthu wolakwa pomuchitira umboni wonama. “Usatsate gulu la anthu ndi kuchita choyipa. Pamene ukupereka umboni mʼbwalo lamilandu, usakhotetse mlandu chifukwa chofuna kukondweretsa anthu ambiri. Ndipo poweruza mlandu wa munthu wosauka usamukondere. “Ngati ukumana ndi ngʼombe kapena bulu wa mdani wako zitasochera, uwonetsetse kuti wazitenga kupita nazo kwa mwini wakeyo. Ngati uwona bulu wa munthu wina amene amakuda atagwa ndi katundu, usamusiye pomwepo, uwonetsetse kuti wamuthandiza. “Usakhotetse milandu ya anthu osauka. Upewe zabodza ndipo usaphetse munthu wosalakwa ndi wolungama, chifukwa Ine sindidzakhululukira wochimwa. “Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. “Usamuzunze mlendo, pakuti inu nomwe mukudziwa mmene amamvera mlendo chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Igupto. Malamulo a Nthawi Zopuma “Muzidzala mbewu zanu mʼmunda ndi kumakolola mbewuzo kwa zaka zisanu ndi chimodzi. Koma chaka chachisanu ndi chiwiri muzisiya osalima mindayo kuti anthu osauka pakati panu azipezamo chakudya, ndipo nyama zakuthengo zizidya zotsalazo. Muzichita chimodzimodzi ndi minda ya mpesa ndi mitengo ya olivi. “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri musagwire ntchito kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu apume ndiponso kuti kapolo wobadwira mʼnyumba yanu ndi mlendo yemwe apezenso mphamvu. “Samalani pochita zonse zimene ine ndanena. Musamapemphere kwa milungu ina ndipo mayina awo musamawatchule. Masiku Atatu Akulu a Chikondwerero “Muzichita zikondwerero zolemekeza Ine katatu pa chaka. “Muzichita Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi mwezi wa Abibu pa nthawi yomwe ndayika, pakuti mʼmwezi umenewu munatuluka mʼdziko la Igupto. “Pasapezeke munthu wobwera pamaso panga wopanda kanthu mʼmanja. “Muzichita Chikondwerero cha Masika pogwiritsa ntchito zipatso zoyambirira kucha zimene munadzala mʼmunda. “Muzichitanso Chikondwerero cha Zokolola pakutha pa chaka, pamene mukututa zokolola zanu mʼmunda. “Amuna onse azionekera pamaso pa Ambuye Yehova katatu pa chaka. “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti. “Ndipo musasunge mafuta anyama yansembe ya pa chikondwerero mpaka mmawa. “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake. Kutsogolera kwa Mngelo wa Mulungu “Taona Ine ndikutuma mngelo wanga patsogolo panu kuti akutetezeni mʼnjiramo ndi kukakufikitsani ku malo amene ndakonza. Muzimumvera ndi kumvetsetsa zimene akunena. Musamuwukire chifukwa sadzakhululuka kuwukira kwanu, pakuti akuchita zimenezi mʼdzina langa. Ngati mudzamvera iyeyu ndi kuchita zonse zimene Ine ndikunena, Ine ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzatsutsana ndi onse otsutsana nanu. Mngelo wanga adzakhala patsogolo panu ndipo adzakufikitsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanaani, Ahivi ndi Ayebusi, ndipo ndidzawapheratu onsewo. Musagwadire milungu yawo kapena kuyipembedza. Ndipo musatsatire zinthu zomwe amachita. Koma inu mukawononge milungu yawo ndi kuphwasula malo amene amapembedzerapo. Muzipembedza Yehova Mulungu wanu ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi ndiponso ndidzachotsa nthenda pakati panu. Palibe mkazi amene adzapite padera kapena kukhala wosabereka mʼdziko mwanu. Ndidzakupatsani moyo wautali. “Ine ndidzawachititsa mantha ndi kusokoneza anthu onse amene adzalimbana ndi inu ndipo adani anu onse adzakuthawani. Ahivi, Akanaani ndi Ahiti adzathawa ngati kuti ndawatumizira mavu. Komabe sindidzawachotseratu onse mʼchaka chimodzi chifukwa dziko lingadzakhale lopanda anthu ndipo nyama zakuthengo zidzakuchulukirani. Ndidzawathamangitsa pangʼonopangʼono mpaka inu mutachuluka kokwanira mwakuti nʼkutenga dzikolo. “Malire a dziko lanu adzakhala kuyambira ku Nyanja Yofiira mpaka ku nyanja ya Afilisti, ndiponso kuyambira ku chipululu mpaka ku mtsinje wa Yufurate. Anthu onse okhala mʼdziko limeneli ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo mudzawathamangitsa. Musachite pangano ndi iwo kapena ndi milungu yawo. Asadzakhale mʼdziko lanu chifukwa angadzakuchimwitseni ndi kuyamba kupembedza milungu yawo. Mukadzatero ndiye kuti mwakodwa mu msampha.” Kutsimikizira kwa Pangano Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Bwera ku phiri kuno kwa Yehova, iwe pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu a Israeli makumi asanu ndi awiri. Enanu mundipembedze muli chapatali. Koma Mose yekha ayandikire Yehova, ndipo enawo asayandikire. Komanso anthu ena onse asakwere nawe ku phiri kuno.” Tsono Mose anapita kukawuza anthu mawu onse a Yehova ndi malamulo onse, ndipo anthu onse anayankha mogwirizana kuti, “Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Ndipo Mose analemba zonse zimene Yehova ananena. Mmawa mwake Mose anadzuka nayamba kumanga guwa lansembe mʼmunsi mwa phirilo ndipo anayimika miyala khumi ndi iwiri ngati zipilala kuyimira mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Kenaka Mose anatuma Aisraeli achinyamata kuti aphe ndi kukapereka kwa Yehova nsembe zopsereza zachiyanjano. Mose anatenga theka la magazi ndi kuyika mʼmbale, ndipo theka linalo analiwaza pa guwa lansembe. Anatenganso Buku la Chipangano ndi kuwerengera anthu. Anthuwo anayankha kuti, “Zonse zimene Yehova wanena tamva, ndipo tidzazichita.” Kenaka Mose anatenga magazi, nawaza anthuwo ndipo anati, “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapanga ndi inu molingana ndi mawu ake onsewa.” Kenaka Mose pamodzi ndi Aaroni, Nadabu, Abihu ndi akuluakulu makumi asanu ndi awiri a Israeli aja anakwera ku phiri, ndipo anaona Mulungu wa Israeli. Pansi pa mapazi ake panali njira yoyendamo yopangidwa ndi mwala wa safiro woyalidwa bwino wa maonekedwe owala ngati thambo. Ngakhale anaona Yehova koma sanafe, mʼmalo mwake anadya ndi kumwa. Yehova anati kwa Mose, “Bwera kwa ine ku phiri kuno, ndipo udikire konkuno. Ndidzakupatsa miyala imene ndalembapo malemba kuti ndiwaphunzitse.” Ndipo anayamba ulendo wopita ku phiri la Mulungu pamodzi ndi womuthandiza wake Yoswa. Apa nʼkuti Mose atawawuza akuluakulu aja kuti, “Mudikire pano mpaka titabweranso. Aaroni ndi Huri ali nanu, aliyense amene ali ndi milandu apite kwa iwo.” Mose atakwera ku phiri kuja mtambo unaphimba phirilo. Ulemerero wa Yehova unakhala pa phiri la Sinai, ndipo mtambo unaphimba phirilo kwa masiku asanu ndi limodzi. Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri Yehova anayitana Mose kuchokera mu mtambowo. Ulemerero wa Yehova uja unkaoneka ngati malawi a moto pamwamba pa phirilo. Ndipo Mose analowa mʼmitambo nakwera phiri. Iye anakhala ku phiriko 40 usana ndi usiku. Zopereka Zomangira Chihema Yehova ananena kwa Mose kuti, “Uza Aisraeli kuti abweretse chopereka kwa Ine. Iwe ulandire choperekacho mʼmalo mwanga kuchokera kwa munthu amene akupereka mwakufuna kwake. Zopereka zimene ulandire kwa anthuwo ndi izi: Golide, siliva ndi mkuwa. Nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa, ubweya wambuzi; zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha; mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa efodi ndi pa chovala cha pachifuwa. “Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. Umange chihema ndiponso ziwiya zamʼkatimo monga momwe Ine ndidzakuonetsere. Bokosi la Chipangano “Tsono apange bokosi lamatabwa amtengo wa mkesha, ndipo kutalika kwake kukhale masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. Bokosilo ulikute ndi golide wabwino kwambiri, mʼkati mwake ndi kunja komwe, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. Upange mphete zinayi zagolide ndipo uzimangirire ku miyendo yake inayi ya bokosilo, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. Kenaka upange mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. Ndipo ulowetse nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. Nsichizo zizikhala mʼmphete za bokosilo nthawi zonse, zisamachotsedwe. Ndipo udzayike mʼbokosilo miyala iwiri yolembedwapo malamulo imene Ine ndidzakupatse. “Upange chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. Ndipo upange Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo, uwayike mbali ziwiri za chivundikirocho, kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa uwapangire limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. Mapiko a Akerubiwo adzatambasukire pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo adzakhale choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. Uyike chivundikirocho pamwamba pa bokosi ndipo mʼbokosilo uyikemo miyala ya malamulo, imene ndidzakupatse. Ndizidzakumana nawe pamenepo, pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo, pakati pa Akerubi awiriwo, ndikumadzakupatsa malamulo onse okhudzana ndi Aisraeli. Tebulo la Buledi Woperekedwa kwa Mulungu “Upange tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. Tebulolo ulikute ndi golide wabwino kwambiri ndipo upange mkombero wagolide mʼmbali mwake. Upange feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo uyike mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. Upange mphete zinayi zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya zake zinayi, kumene kuli miyendo yake inayi. Mphetezo uziyike kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. Upange mbale ndi zipande zagolide wabwino, pamodzinso ndi mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe. Pa tebulopo uyikepo buledi woperekedwa kosalekeza, kuti azikhala pamaso panga nthawi zonse. Choyikapo Nyale “Upange choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zikhale zosulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zipangidwire kumodzi. Mʼmbali mwake mukhale mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zikhale pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri pakhalenso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zikhale chimodzimodzi ndipo zituluke mʼchoyikapo nyalecho. Pa choyikapo nyalecho pakhale zikho zinayi zopangidwa ngati maluwa amtowo ali ndi mphukira ndi maluwa. Mphukira yoyamba ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri ikhale mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Ndipo mphukira yachitatu ikhale mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zikhale nthambi zisanu ndi imodzi Mphukira ndi nthambi zonse zisulidwe kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri. “Ndipo upange nyale zisanu ndi ziwiri ndi kuziyika pa choyikapo nyalecho kuti ziwunikire kutsogolo. Mbaniro ndi zowolera phulusa zikhale zagolide wabwino kwambiri. Choyikapo nyale ndi zipangizo zonse zipangidwe ndi golide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. Uwonetsetse kuti wapanga zonse monga momwe ndikukuonetsera pa phiri pano.” Chihema cha Mapemphero “Panga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso apete pa nsaluzo Akerubi. Nsalu zonse zikhale zofanana. Mulitali mwake zikhale mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi. Uchite chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. Panga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Uchitenso chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. Upange zokolowekamo 50 pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Upange motero kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. Kenaka upange ngowe zagolide makumi asanu zolumikizira nsalu ziwirizo kuti zipange chihema chimodzi. “Upange nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zikhale khumi ndi imodzi. Nsalu zonse khumi ndi imodzi zikhale zofanana. Mulitali mwake mukhale mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake mukhale mamita awiri. Ulumikize nsalu zisanu kuti ikhale nsalu imodzi ndipo zina zisanu ndi imodzi uzilumikizenso kuti ikhale nsalu imodzinso. Nsalu yachisanu ndi chimodzi imene ili kutsogolo kwa tenti uyipinde pawiri. Upange zokolowekamo 50 mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija. Upangenso zokolowekamo zina 50 mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. Kenaka upange ngowe 50 zamkuwa ndipo uzilowetse mu zokolowekazo. Ndiye uphatikize nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. Theka lotsalira la nsaluyo lidzalendewera kumbuyo kwa chihemacho. Nsalu yotsalira ya masentimita 46 mulitali mwake mʼmbali zonse ziwiri idzalendewere kuphimba mbali ziwirizo. Upange chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake upangireponso chophimbira china cha zikopa za akatumbu. “Upange maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. Feremu iliyonse ikhale yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake mukhale masentimita 69. Thabwa lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri. Upange maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. Upange maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho. Ndipo upange matsinde 40 asiliva ndipo uwayike pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse pakhale matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. Ndipo mbali yakumpoto ya chihemacho upangenso maferemu makumi awiri. Upangenso matsinde 40 asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. Upange maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo. Ndipo upangenso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. Pa ngodya ziwirizi pakhale maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba ndipo alumikizidwe pa ngowe imodzi. Maferemu onse akhale ofanana. Choncho pakhale maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri akhale pansi pa feremu iliyonse. “Upange mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha: mitanda isanu ikhale ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, mitanda isanu inanso ikhale ya maferemu a mbali inayo. Pakhalenso mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. Mtanda wapakati pa maferemuwo uchokere pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. Maferemuwo uwakute ndi golide ndiponso upange mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso uyikute ndi golide. “Upange chihema mofanana ndi momwe ndinakuonetsera pa phiri paja. “Upange nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo ikhale yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso apetepo zithunzi za Akerubi. Nsaluyo uyikoloweke pa nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide zomwe zili ndi ngowe zagolide, zomwe zayima pa matsinde asiliva anayi. Ukoloweke kataniyo ku ngowe ndipo uyike Bokosi la Chipangano mʼkatimo. Kataniyo idzalekanitse malo wopatulika ndi malo wopatulika kwambiri. Uyike chivundikiro pa bokosi laumboni ku malo wopatulika kwambiri. Uyike tebulo kunja kwa katani yotchinga cha kumpoto kwa chihema ndipo uyike choyikapo nyale chija kummwera moyangʼanana ndi tebulolo. “Pa chipata cholowera mu chihema, uyikepo nsalu yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira, yomwe ndi yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. Upange ngowe zagolide za nsaluyo ndi nsanamira zisanu zamtengo wa mkesha ndipo uzikute ndi golide. Upangenso matsinde asanu amkuwa a nsanamirazo.” Guwa Lansembe Yopsereza “Upange guwa lansembe lamatabwa amtengo wa mkesha. Likhale lofanana mbali zonse, msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi mwake masentimita 229. Upange nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo kuti nyangazo ndi guwalo zikhale chinthu chimodzi, ndipo ulikute guwalo ndi mkuwa. Upange ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika yochotsera phulusa, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. Upange sefa yachitsulo chamkuwa ndipo mʼngodya zake zinayizo upangiremo mphete zamkuwa. Uyike sefayo mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, ndipo ilekezere pakati pa guwa lansembelo. Upange nsichi zamtengo wa mkesha ndipo uzikutire ndi mkuwa. Pamene mukunyamula guwalo, muzilowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo. Guwalo likhale lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Ulipange monga momwe ndinakuonetsera pa phiri paja. Za Bwalo la Chihema “Upange bwalo la chihema. Mbali yakummwera ikhale yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. Upangenso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa, ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. Mbali yakumpoto ikhalenso yotalika mamita 46 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga. Pakhalenso mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. “Mbali yakumadzulo ya bwalolo ikhale yotalika mamita 23 ndipo ikhale ndi nsalu yotchinga, nsichi khumi ndi matsinde khumi. Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, kutalika kwa bwalo kukhale mamita 23. Mbali imodzi yachipata kukhale nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu. Ndipo ku mbali inayo kukhale nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu. “Pa chipata cha bwalolo pakhale nsalu yotchinga yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira ndiponso yofewa yosalala. Nsaluyo ikhale yotalika mamita asanu ndi anayi, yopangidwa ndi anthu aluso. Pakhalenso mizati yake inayi ndi matsinde akenso anayi. Mizati yonse yozungulira bwalolo ilumikizidwe ndi zingwe zasiliva. Ngowe zake zikhale zasiliva, koma matsinde ake akhale amkuwa. Kutalika kwa bwalolo kukhale mamita 46, mulifupi mwake mamita 23, msinkhu wake masentimita 230. Nsalu ya katani ikhale yofewa ndi yosalala bwino. Matsinde ake akhale amkuwa. Zipangizo zonse zogwiritsa ntchito zosiyanasiyana pa chihemacho, zikhomo za chihema ndi zabwalolo zikhale zamkuwa. Mafuta Anyale “Lamula Aisraeli kuti akupatse mafuta anyale a olivi wabwino kwambiri kuti nyalezo ziziyaka nthawi zonse. Mʼchihema cha msonkhano, koma kunja kwa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano, Aaroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale ikukhala chiyakire pamaso pa Yehova kuyambira madzulo mpaka mmawa. Limeneli ndi lamulo lamuyaya pakati pa Aisraeli pa mibado yonse.” Zovala za Ansembe “Aaroni mʼbale wako ndi ana ake aamuna, Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara uwapatule pakati pa Aisraeli. Abwere kwa iwe kuti anditumikire monga ansembe. Umusokere mʼbale wako, Aaroni, zovala zopatulika kuti azioneka mwaulemerero ndi molemekezeka. Uwawuze anthu onse aluso amene Ine ndawapatsa nzeru pa ntchito yosoka kuti apange zovala za Aaroni za pa mwambo womupatula, kuti iye anditumikire monga wansembe. Zovala zoti apange ndi izi: chovala chapachifuwa, efodi, mkanjo, mwinjiro wolukidwa, nduwira ndi lamba. Apangire mʼbale wako Aaroni ndi ana ake aamuna zovala zopatulikazi kuti iwo anditumikire monga ansembe. Iwo agwiritse ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira ndi yosalala yofewa. Efodi “Apange efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yolukidwa mwaluso. Efodiyo ikhale ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. Lamba womangira efodi akhale wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Akhale wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala. “Utenge miyala iwiri ya onikisi ndipo uzokotepo mayina a ana a Israeli. Mayina asanu ndi limodzi akhale pa mwala umodzi, ndipo mayina asanu ndi limodzi pa mwala winawo motsata mabadwidwe awo. Mayina a ana a Israeli uwazokote pa miyala iwiriyo, monga momwe amachitira mmisiri wozokota miyala. Ndipo uyike miyalayo mu zoyikamo zake zagolide. Umangirire miyala iwiriyi pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli. Aaroni azinyamula mayinawo mʼmapewa ake kuti akhale chikumbutso pamaso pa Yehova. Upange zoyikamo za maluwa agolide, ndiponso maunyolo awiri a golide wabwino kwambiri, wopetedwa ngati zingwe ndipo uwalumikize ku zoyikamozo. Chovala Chapachifuwa “Upange chovala chapachifuwa chogwiritsa ntchito poweruza mlandu ndipo uchipange mwaluso kwambiri. Uchipange ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. Kutalika kwake kukhale kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, ndipo chikhale chopinda pawiri. Uyikepo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rubi, topazi ndi berili. Mzere wachiwiri pakhale miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; mzere wachitatu pakhale miyala ya opera, agate ndi ametisiti. Mzere wachinayi pakhale miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi uyiike mu zoyikamo zagolide. Miyalayo ikhalepo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse uzokotedwe ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli. “Upange timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. Upangenso mphete ziwiri zagolide ndipo uzimangirire pa ngodya ziwiri za pa chovala chapachifuwa. Umangirire timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. Ndipo mbali ina ya timaunyoloto umangirire pa zoyikapo zake ziwiri zija ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. Upangenso mphete ziwiri zagolide, ndipo uzilumikize ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. Upangenso mphete zina ziwiri zagolide ndipo uzilumikize kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. Tsono umangirire mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi. “Pamene Aaroni akulowa kumalo opatulika azivala chovala chapachifuwa cha zoweruzira chija chimene chalembedwa mayina a ana a Israeli kuti Yehova awakumbukire nthawi zonse. Ndiponso uyike Urimu ndi Tumimu mu chovala chapachifuwa cha zoweruziracho, kuti zikhale pamtima pa Aaroni. Choncho Aaroniyo adzakhala akutenga nthawi zonse zida zomuthandizira kuweruza ana a Israeli pamene adzafika pamaso pa Yehova. Zovala Zina za Ansembe “Uyipangire efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo. Mkanjowo ukhala ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo pakhale chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, upange mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira zokhala ndi maberu agolide pakati pake. Choncho pazikhala mphonje imodzi kenaka belu limodzi, kuzungulira mpendero wa mkanjo wonse. Aaroni azivala mkanjowo pamene akutumikira ngati wansembe. Kulira kwa maberu kuzimveka pamene akulowa mʼmalo opatulika pamaso pa Yehova ndiponso pamene akutuluka, kuti asafe. “Upange duwa lagolide wabwino kwambiri kukhala ngati chidindo ndipo uzokotepo mawu akuti, Cohoperekedwa kwa Yehova. Ulimange ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira ya Aaroni, ndipo duwalo likhale kutsogolo kwa nduwirayo. Lidzakhala pa mphumi ya Aaroni, motero iye adzasenza cholakwa chilichonse cha pa zopereka zilizonse zimene Aisraeli amazipatulira Yehova. Aaroni azivala chikwangwanichi pa mphumi pake nthawi zonse kuti Yehova alandire zopereka za anthu ake. “Uluke mwinjiro wa nsalu yofewa yosalala ndiponso upange nduwira ya nsalu yofewa yosalala. Lamba wake akhale wolukidwa bwino ndi munthu waluso. Upangirenso ana a Aaroni mwinjiro, malamba ndi nduwira kuti azioneka mwaulemu ndi molemekezeka. Zovala zimenezi umuveke Aaroni, mʼbale wako ndi ana ake. Kenaka uwadzoze, uwapatse udindo ndi kuwapatula kuti anditumikire ngati ansembe anga. “Uwapangire akabudula a nsalu yofewa oyambira mʼchiwuno kulekeza mʼntchafu kuti asamaonetse maliseche. Aaroni ndi ana ake ayenera kuvala akabudulawo pamene akulowa mu tenti ya msonkhano kapena pamene akupita ku guwa lansembe kukatumikira malo oyera kuopa kuti angachimwe ndi kufa. “Ili likhale lamulo la nthawi zonse kwa Aaroni ndi zidzukulu zake.” Mwambo Wopatula Ansembe “Pofuna kumupatula Aaroni ndi ana ake kuti akhale ansembe onditumikira Ine, uchite izi: Utenge ngʼombe yayingʼono yayimuna ndi nkhosa ziwiri zazimuna zopanda chilema. Utengenso buledi wopanda yisiti, makeke wopanda yisiti wopakidwa mafuta. Zonsezi uzipange ndi ufa wosalala wa tirigu. Uziyike mʼdengu ndipo ubwere nazo kwa Ine pamodzi ndi ngʼombe yayimuna ija ndi nkhosa ziwiri zazimuna zija. Kenaka ubwere naye Aaroni ndi ana ake pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. Tenga zovala ndipo umuveke Aaroni mwinjiro, mkanjo wa efodi, efodiyo ndi chovala chapachifuwa. Umumange mʼchiwuno lamba wa efodi wolukidwa mwaluso uja. Umuveke nduwira kumutu, ndiponso uyike chizindikiro chopatulika chija pa nduwirayo. Utenge mafuta wodzozera ndipo uwatsanulire pamutu pake kumudzoza. Ubwere ndi ana ake aamuna ndipo uwavekenso minjiro ndi nduwira. Kenaka umange malamba Aaroniyo pamodzi ndi ana ake ndi kuwaveka nduwira. Motero unsembe udzakhala wawo malingana ndi lamulo ili losatha. “Umu ndi mmene udzadzozere Aaroni ndi ana ake aamuna. “Ubwere ndi ngʼombe yayimuna pa khomo la tenti ya msonkhano ndipo Aaroni ndi ana ake asanjike manja awo pamutu pake. Uphe ngʼombeyo pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Utenge magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chako pa nyanga zaguwa lansembe ndipo magazi otsalawo uwakhutulire pa tsinde laguwalo. Kenaka utenge mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake. Zonsezi uzitenthe pa guwapo. Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake uziwotche kunja kwa msasa. Iyi ndi nsembe yopepesera machimo. “Utenge nkhosa yayimuna imodzi ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. Uyiphe ndipo utenge magazi ake ndi kuwaza mbali zonse zaguwalo. Uyidule nkhosayo nthulinthuli, kutsuka matumbo ake ndi miyendo yake. Ukatero, pamodzi ndi mutu wake, uziyike pamwamba pa nthulizo. Ndipo uwotche nkhosa yonseyo pa guwa lansembe. Iyi ndi nsembe yopsereza ya kwa Yehova. Ili ndi fungo lokoma, loperekedwa pa moto kwa Yehova. “Utenge nkhosa yayimuna ina ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna asanjike manja awo pamutu pake. Uyiphe ndipo utenge magazi ake ena ndi kupaka ndewere za makutu a kudzanja lamanja la Aaroni ndi ana ake aamuna. Upakenso pa zala zawo zazikulu za kudzanja lawo lamanja, ndi zala zazikulu za kuphazi lakudzanja lawo lamanja. Kenaka uwaze magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. Ndipo utenge magazi ena amene ali pa guwa lansembe komanso pa mafuta ena odzozera ndipo uwawaze pa Aaroni ndi zovala zake ndi ana ake ndi zovala zawo. Ndiye kuti iyeyo ndi ana ake aamuna adzakhala opatulika pamodzi ndi zovala zawo. “Pa nkhosa yayimuna ija utengepo mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake, ndiponso ntchafu yakumanja. Iyi ndi nkhosa ya mwambo wodzoza. Utengenso mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene lili pamaso pa Yehova, buledi mmodzi, buledi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. Izi zonse uzipereke mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake, ndipo iwo aziweyule pamaso pa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. Kenaka uzitenge mʼmanja mwawo ndipo uzipsereze pa guwa lansembe, pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza kuti ipereke fungo lokoma kwa Yehova. Ichi ndiye chopereka chachakudya kwa Yehova. Kenaka utenge chidale cha nkhosa yayimuna imene inaperekedwa pamwambo wodzoza Aaroni, uchiweyule kuti chikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova ndipo chidzakhala gawo lako. “Uzipatule ziwalo zonse za nkhosa ya pa mwambo wodzoza Aaroni ndi ana ake. Chidale chimene unaweyula chija ndiponso ntchafu imene inaperekedwa ija. Nsembe izi ndi zimene Aisraeli azipereka kwa Aaroni ndi ana ake mwa zonse zimene azipereka nthawi zonse. Mwa zopereka za mtendere zimene ana a Aisraeli adzapereka kwa Yehova, zimenezi zikhale gawo lawo. “Zovala zopatulika za Aaroni zidzakhala za ana ake aamuna iye atafa kuti adzavale podzozedwa ndi polandira udindo wawo. Mwana amene adzalowa mʼmalo mwake monga wansembe pamene adzabwerera kudzalowa mu tenti ya msonkhano kudzatumikira ku malo wopatulika, adzavala zovala zimenezi masiku asanu ndi awiri. “Utenge nkhosa yayimuna ya pamwambo wodzoza ansembe ndipo uyiphike pamalo opatulika. Aaroni ndi ana ake adye nyama ya nkhosa yayimunayi pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu pa khomo la tenti ya msonkhano. Adye zonse zimene anazipereka kwa Yehova pamwambo wopepesera machimo powadzoza ndi kuwapatula. Munthu wamba asadye chifukwa ndi zopatulika. Ndipo ngati nyama ina ya nkhosa ya pamwambo wodzoza ansembe kapena buledi zatsala mpaka mmawa, muziwotche, asazidye chifukwa ndi zopatulika. “Uchitire Aaroni ndi ana ake aamuna zonse zimene ndakulamulazi. Uchite mwambo wowapatula kukhala ansembe masiku asanu ndi awiri. Tsiku lililonse uzipereka ngʼombe yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo kuti machimowo akhululukidwe. Ndiponso upatule guwalo popereka nsembe yopepesera ndi kulidzoza mafuta kuti likhale lopatulika. Pa masiku asanu ndi awiri uzipereka pa guwapo nsembe zoyeretsera guwalo, ukatero ndiye kuti uzilipatula. Ndipo guwa lansembelo lidzakhala loyera kwambiri, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza guwalo chidzayeretsedwa. “Tsiku ndi tsiku pa guwa lansembe uzipereka izi: Ana ankhosa a chaka chimodzi awiri. Mmawa muzipereka mwana wankhosa mmodzi ndipo winayo madzulo. Pamodzi ndi mwana wankhosa woyambayo, muzipereka kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi lita imodzi ya mafuta a olivi pamodzi ndi lita imodzi ya vinyo ngati chopereka chachakumwa. Upereke mwana wankhosa winayo madzulo pamodzi ndi chopereka chachakudya monga poyamba paja ndi chopereka chachakumwa monga mmawa kuti ikhale fungo lokoma la chopereka chachakudya kwa Yehova. “Zopereka zopsereza zimenezi ziziperekedwa nthawi zonse, pa mibado yonse. Muzidzazipereka pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano. Pa guwa lansembe, Yehova adzakumana nanu ndi kuyankhula nanu. Pameneponso Ine ndidzakumana ndi Aisraeli, ndipo guwalo lidzakhala lopatulika chifukwa cha ulemerero wanga. “Tsono Ine ndidzapatula tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe. Ndidzapatulanso Aaroni pamodzi ndi ana ake kuti akhale ansembe anga onditumikira. Ndidzakhala pakati pa Aisraeli ndikukhala Mulungu wawo. Adzadziwa kuti ine ndine Mulungu wawo amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto kuti ndikhale pakati pawo. Ine ndine Yehova, Mulungu wawo.” Guwa Lansembe Yofukiza Upange guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. Ukute guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse zinayi, pamodzi ndi nyanga zake. Ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira guwalo. Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo. Upange mizati yamtengo wa mkesha ndipo uyikute ndi golide. Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe. “Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani. Aaroni ayenera kufukizanso lubani pamene ayatsa nyale madzulo kuti lubani akhale akuyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova kwa mibado imene ikubwera. Pa guwapo usafukize lubani wachilendo kapena kuperekapo nsembe yopsereza kapena nsembe yaufa. Usathire pa guwapo ngakhale nsembe yachakumwa. Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.” Za Chopereka Chowombolera Moyo Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga. Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova. Aliyense wolembedwa mu kawundula amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira ayenera kupereka chopereka kwa Yehova. Anthu olemera asapereke koposa theka la sekeli ndipo osauka asapereke kuchepera theka la sekeli pamene mukupereka nsembe kwa Yehova yowombolera miyoyo yanu. Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.” Za Beseni Losambira Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Upange beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso. Uliyike pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi. Aaroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi kutsuka mapazi awo ndi madzi amenewo. Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova, azisamba mʼmanja mwawo ndi kutsuka mapazi kuti asadzafe. Limeneli ndi lamulo limene Aaroni, pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake mʼtsogolomo ayenera kumadzalitsatira mpaka muyaya.” Mafuta Wodzozera Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Utenge zonunkhira bwino kwambiri izi: makilogalamu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogalamu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa sinamoni, makilogalamu atatu a nzimbe yonunkhira bwino kwambiri, makilogalamu asanu ndi limodzi a mkesha. Zonsezi zikhale malingana ndi muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu. Pakhalenso malita anayi a mafuta a olivi. Ugwiritse ntchito zinthu zimenezi kupanga mafuta opatulika odzozera, mafuta onunkhira, apangidwe ndi mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Awa adzakhala mafuta opatulika odzozera. Tsono uwagwiritse ntchito podzoza tenti ya msonkhano, Bokosi la Chipangano, tebulo, ndi ziwiya zake zonse, choyikapo nyale ndi zipangizo zake, guwa lofukizirapo lubani, guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso beseni pamodzi ndi nsichi yake. Zonsezi uzipatule kuti zidzakhale zopatulika, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza zimenezi chidzakhala chopatulika. “Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira. Tsono awuze a Israeli kuti, mafuta wodzozera awa adzakhala wopatulika mpaka muyaya. Musadzadzozere munthu wamba mafuta amenewa, ndipo musadzapange mafuta wofanana ndi amenewa. Mafutawa ndi wopatulika ndipo akhale woyera kwa inu. Wina aliyense amene adzapanga mafuta wonunkhira wofanana nawo kapena kudzozera mafutawa munthu wamba osati wansembe ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.” Za Zofukiza Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tenga muyeso wofanana wa zinthu zonunkhira izi: sitakate, onika, galibanumu pamodzi ndi lubani weniweni. Uziphatikize pamodzi zonsezi ndi kupanga lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athire mchere ndipo akhale woyera ndi wopatulika. Upere gawo lina mosalala kwambiri ndipo utapepo pangʼono ndi kuyika patsogolo pa Bokosi la Chipangano mu tenti ya msonkhano, kumene ine ndidzakumane nawe. Lubani ameneyu kwa inu adzakhala wopatulika kwambiri. Musapange lubani wanu potsatira njira iyi. Lubani yense wopangidwa mwa njira iyi akhale wopatulika, woperekedwa kwa Yehova. Aliyense amene adzapanga wofanana naye kuti asangalale ndi fungo lake ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.” Bezaleli ndi Oholiabu Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Taona, ndasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda. Ndipo ndamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. Ndasankhanso Oholiabu mwana wa Ahisamaki wa fuko la Dani. Ndiponso ndapereka nzeru kwa anthu aluso motero adzagwira ntchito zonse zimene ndakulamulira kuti zichitike monga izi: Kupanga tenti ya msonkhano, bokosi laumboni pamodzi ndi chophimbira chake, ndiponso zonse za mu tenti, tebulo ndi zida zake, choyikapo nyale cha golide wabwino kwambiri ndi ziwiya zake zonse, guwa lofukizirapo lubani, guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, beseni ndi nsichi yake, ndiponso zovala zonse zolukidwa, zovala zopatulika za Aaroni wansembe pamodzi ndi za ana ake, zovala pamene akutumikira monga ansembe, ndiponso mafuta odzozera ndi lubani wonunkhira wa ku malo opatulika. Iwo azipanga monga momwe Ine ndinakulamulira.” Za Sabata Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Uza ana a Israeli kuti azisunga Masabata anga. Ichi chidzakhala chizindikiro pakati pa inu ndi Ine pamodzi ndi zidzukulu zanu mʼtsogolomo, chosonyeza kuti Ine ndine amene ndimakuyeretsani. “Motero muzisunga tsiku la Sabata chifukwa ndi loyera kwa inu. Aliyense amene adetsa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake. Mugwire ntchito kwa masiku asanu ndi limodzi koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, lopuma, tsiku lopatulika la Yehova. Aliyense amene agwira ntchito iliyonse pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. Aisraeli onse komanso zidzukulu zawo mʼtsogolo azidzasunga tsiku la Sabata ngati pangano lamuyaya. Tsiku la Sabata lidzakhala chizindikiro chamuyaya pakati pa Ine ndi Aisraeli chosonyeza kuti Yehova analenga za kumwamba ndi dziko lapansi kwa masiku asanu ndi limodzi ndi kuti pa tsiku lachisanu ndi chiwiri analeka kugwira ntchito napumula.” Yehova atamaliza kuyankhula ndi Mose pa phiri la Sinai, anamupatsa Mose miyala iwiri yaumboni, imene Mulungu analembapo ndi chala chake. Za Fano la Mwana Wangʼombe Wagolide Anthu ataona kuti Mose akuchedwa kutsika mʼphiri, anasonkhana kwa Aaroni ndipo anati, “Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.” Aaroni anawayankha kuti, “Vulani ndolo zagolide zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi aakazi ndipo muzibweretse kwa ine.” Kotero anthu onse anavula ndolo zagolide ndi kubwera nazo kwa Aaroni. Choncho Aaroni analandira golideyo ndipo anamuwumba ndi chikombole ndi kupanga fano la mwana wangʼombe. Kenaka anthu aja anati, “Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.” Aaroni ataona izi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa mwana wangʼombeyo ndipo analengeza kuti, “Mawa kudzakhala chikondwerero cha Yehova.” Kotero tsiku linalo anthu anadzuka mmamawa ndithu ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Atatha kupereka nsembezo, anthuwo anakhala pansi nayamba kudya ndi kumwa. Kenaka anayimirira nayamba kuvina mwachilendo. Pamenepo Yehova anati kwa Mose, “Tsika msanga, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto aja adziyipitsa kwambiri. Iwo apatuka mwamsanga kuleka kutsatira zimene ndinawalamula. Ndiye adzipangira fano la mwana wangʼombe. Aligwadira ndi kuliperekera nsembe nʼkumati, ‘Inu Aisraeli, nayu mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto.’ ” Yehova anati kwa Mose, “Ine ndikuwadziwa anthu amenewa. Iwowa ndi ankhutukumve. Chifukwa chake undileke kuti mkwiyo wanga uyake pa iwo ndi kuwawononga. Ndipo Ine ndidzakusandutsa kuti ukhale mtundu waukulu.” Koma Mose anapempha chifundo cha Mulungu wake ndipo anati, “Chonde Yehova, chifukwa chiyani mwakwiyira anthu awa amene munawatulutsa mʼdziko la Igupto ndi mphamvu yanu yayikulu ndi dzanja lanu lamphamvu. Kodi mukufuna kuti Aigupto azinena kuti, ‘Munali ndi cholinga choyipa chofuna kuwaphera ku mapiri kuno ndi kuwawonongeratu pa dziko lapansi pamene munkawatulutsa ku Igupto kuja?’ Ayi, chonde mkwiyo wanu woyaka ngati motowu ubwezeni ndipo sinthani maganizo ofunira zoyipa anthu anu. Kumbukirani atumiki anu, Abrahamu, Isake, Israeli ndi zija munawalonjeza polumbira pa dzina lanu kuti, ‘Ine ndidzachulukitsa zidzukulu zanu ndipo zidzakhala zambiri ngati nyenyezi zakumwamba. Zidzukulu zanuzo ndidzazipatsa dziko lonseli limene ndinalonjeza. Dziko limeneli lidzakhala lawo nthawi zonse.’ ” Choncho Yehova analeka ndipo sanawachitire choyipa anthu ake monga anaopsezera. Mose anatembenuka ndi kutsika phiri miyala iwiri ya pangano ili mʼmanja mwake. Miyalayi inalembedwa mbali zonse, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. Miyalayi anayikonza ndi Mulungu. Malembawo analemba ndi Mulungu mozokota pa miyalapo. Pamene Yoswa anamva phokoso la anthu anati kwa Mose, “Ku msasa kuli phokoso la nkhondo.” Mose anayankha kuti, “Phokoso limeneli sindikulimva ngati phokoso la opambana nkhondo, kapena kulira kwa ongonjetsedwa pa nkhondo. Koma ndikulimva ngati phokoso la anthu amene akuyimba.” Mose atayandikira msasa ndi kuona mwana wangʼombe ndiponso kuvina, anakwiya kwambiri ndipo anaponya pansi miyala imene inali mʼmanja mwake, ndi kuyiphwanya pa tsinde la phiri. Ndipo iye anatenga mwana wangʼombe amene anthu anapanga uja ndi kumuwotcha pa moto ndi kumuperapera ndikukhala ngati fumbi. Kenaka anawaza fumbilo mʼmadzi ndi kuwamwetsa Aisraeli madziwo. Tsono Mose anafunsa Aaroni kuti, “Kodi anthu awa anakuchita chiyani kuti uwachimwitse koopsa chotere?” Aaroni anayankha kuti, “Musakwiye mbuye wanga. Inu mukudziwa kuti anthu awa ndi ovuta. Iwo anati kwa ine, ‘Bwera utipangire milungu imene idzititsogolera. Kunena za Mose amene anatitulutsa ife mʼdziko la Igupto, sitikudziwa chimene chamuchitikira.’ Choncho ine ndinawawuza kuti, ‘Aliyense amene ali ndi zokometsera zagolide azivule.’ Choncho iwo anandipatsa golide, ndipo ndinamuponya pa moto ndi kupanga fano la mwana wangʼombeyu.” Mose anaona kuti anthuwo anali osokonezekadi chifukwa Aaroni anawalekerera mpaka kusanduka anthu osekedwa pakati pa adani awo. Choncho iye anayima pa chipata cholowera mu msasa ndipo anati, “Aliyense amene ali mbali ya Yehova abwere kwa ine.” Ndipo Alevi onse anapita mbali yake. Ndipo iye anawawuza kuti, “Izi ndi zimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena, ‘Pitani ku misasa konse, mulowe ku zipata zonse ndipo aliyense akaphe mʼbale wake, kapena mnzake kapena mnansi wake.’ ” Alevi anachita zomwe Mose analamula, ndipo tsiku limenelo panafa anthu pafupifupi 3,000. Kenaka Mose anati, “Lero mwadzipatula nokha kukhala ansembe otumikira Yehova. Mwachita izi popeza aliyense wa inu wapha mwana wake kapena mʼbale wake. Tsono lero Yehova wakudalitsani.” Mmawa mwake Mose anati kwa anthu onse, “Inu mwachita tchimo lalikulu. Koma tsopano ine ndipita ku phiri kwa Yehova mwina ndikatha kukupepeserani chifukwa cha tchimo lanu.” Kotero Mose anabwereranso kwa Yehova ndipo anati, “Aa! Anthu awa achita tchimo lalikulu! Iwo adzipangira milungu yagolide. Koma tsopano, chonde akhululukireni tchimo lawo. Ngati simutero, ndiye mundifute ine mʼbuku limene mwalemba.” Yehova anamuyankha Mose kuti, “Ndidzafuta mʼbuku aliyense amene wandichimwira. Tsopano pita ukawatsogolere anthu kumalo kumene ine ndinanena, ndipo mngelo wanga adzakutsogolerani. Komabe, nthawi yanga ikadzafika kuti ndiwalange, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.” Ndipo Yehova anawakantha anthuwo ndi mliri chifukwa anawumiriza Aaroni kuti awapangire fano la mwana wangʼombe. Ndipo Yehova anati, “Chokani pa malo ano, iwe ndi anthu amene unawatulutsa mʼdziko la Igupto. Pitani ku dziko limene ine ndinalonjeza ndi lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo kuti, ‘Ine ndidzalipereka kwa zidzukulu zanu.’ Ndipo ndidzatumiza mngelo patsogolo panu kuthamangitsa Akanaani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi. Pitani ku dziko loyenda mkaka ndi uchi. Koma ine sindidzapita nanu, chifukwa anthu inu ndinu nkhutukumve ndipo nditha kukuwonongani mʼnjiramo.” Anthu atamva mawu owopsawa, anayamba kulira ndipo palibe anavala zodzikometsera. Pakuti Yehova anali atanena kwa Mose kuti, “Awuze Aisraeli kuti, ‘Inu ndinu nkhutukumve.’ Ngati ine ndipita ndi inu kwa kanthawi, nditha kukuwonongani. Tsopano vulani zodzikometsera zanu ndipo ine ndidzaganiza choti ndichite nanu.” Kotero Aisraeli anavula zodzikometsera zawo pa phiri la Horebu. Tenti ya Msonkhano Tsono Mose ankatenga tenti ndi kukayimanga kunja kwa msasa chapatalipo, ndipo ankayitcha “tenti ya msonkhano.” Aliyense wofuna kukafunsa kanthu kwa Yehova amapita ku tenti ya msonkhano kunja kwa msasa. Ndipo nthawi ina iliyonse imene Mose amapita ku tenti anthu onse amanyamuka ndi kuyimirira pa makomo amatenti awo, kumuyangʼana Mose mpaka atalowa mu tentimo. Mose akamalowa mu tenti, chipilala cha mtambo chimatsika ndi kukhala pa khomo pamene Yehova amayankhula ndi Mose. Nthawi zonse anthu akaona chipilala cha mtambo chitayima pa khomo la tentiyo amayimirira ndi kupembedza, aliyense ali pa khomo la tenti yake. Yehova amayankhula ndi Mose maso ndi maso ngati mmene munthu amayankhulira ndi bwenzi lake. Kenaka Mose amabwerera ku msasa koma womuthandiza wake, Yoswa, mwana wa Nuni samachoka pa tentiyo. Mose ndi Ulemerero wa Yehova Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ Ngati mwakondwera nane ndiphunzitseni njira zanu kuti ndikudziweni ndi kupitiriza kupeza chisomo pamaso panu. Kumbukirani kuti mtundu uwu ndi anthu anu.” Yehova anayankha kuti, “Ine ndemwe ndidzapita pamodzi ndi iwe, ndipo ndidzakupatsa mpumulo.” Kenaka Mose anati kwa Yehova, “Ngati inu simupita nafe, musatitumize kuti tipite, kutichotsa pano. Kodi wina adzadziwa bwanji kuti inu mwandikomera mtima pamodzi ndi anthu awa ngati simupita nafe? Kodi nʼchiyani chomwe chidzatisiyanitse pakati pa anthu onse amene ali pa dziko lapansi?” Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Ine ndidzachita zimene iwe wandipempha chifukwa Ine ndikukondwera nawe, ndikukudziwa bwino lomwe.” Kenaka Mose anati, “Tsopano ndionetseni ulemerero wanu.” Ndipo Yehova anati, “Ine ndidzakuonetsa ulemerero wanga wonse ndipo ndidzatchula dzina langa lakuti Yehova pamaso pako. Ine ndidzachitira chifundo amene ndikufuna kumuchitira chifundo ndipo ndidzakomera mtima amene ndikufuna kumukomera mtima.” Iye anati, “Koma iwe sungaone nkhope yanga, pakuti palibe munthu amene amaona Ine nakhala ndi moyo.” Ndipo Yehova anati, “Pali malo pafupi ndi ine pomwe ungathe kuyima pa thanthwe. Pamene ulemerero wanga udutsa, ndidzakuyika mʼphanga la thanthwe ndi kukuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. Kenaka ine ndidzachotsa dzanja langa ndipo iwe udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sidzaoneka.” Miyala ina Yatsopano Yehova anati kwa Mose, “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo Ine ndidzalembapo mawu amene anali pa miyala yoyamba ija, imene unayiphwanya. Ukonzeke mmamawa, ndipo ubwere ku Phiri la Sinai. Udzaonekera pamaso panga pamwamba pa phiri. Palibe amene abwere nawe kapena kuoneka pena paliponse pafupi ndi phiri. Ndipo ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmbali mwa phirilo.” Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija ndipo anapita ku Phiri la Sinai mmawa atanyamula miyala iwiri mʼmanja mwake monga momwe Yehova anamulamulira. Ndipo Yehova anatsika mu mtambo ndi kuyima pamodzi ndi Mose ndi kulengeza dzina lake lakuti Yehova. Ndipo Iye anadutsa kutsogolo kwa Mose akulengeza kuti, “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima, wosapsa mtima msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, waonetsa chikondi chosasinthika kwa anthu miyandamiyanda, wokhululukira zoyipa, kuwukira, ndiponso tchimo, komatu salekerera ochimwa kuti asalangidwe. Iye amalanga ana ndi zidzukulu chifukwa cha machimo a makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi.” Pamenepo Mose anawerama pansi napembedza. Iye anati, “Chonde Ambuye, ngati ndapeza chisomo pamaso panu, lolani Ambuye kuti mupite nafe pamodzi. Ngakhale kuti anthuwa ndi nkhutukumve, khululukirani zoyipa ndi machimo athu, ndipo mutenge ife kukhala anthu anu.” Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni. Mverani zimene ndikukulamulirani lero. Ine ndidzathamangitsa pamaso panu Aamori, Akanaani, Ahiti, Aperezi, Ahivi, ndi Ayebusi. Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa mukadzatero iwo adzakhala ngati msampha pakati panu. Mukagumule maguwa awo ansembe, mukaswe miyala yawo yachipembedzo, ndipo mukadule mitengo yawo ya Asera. Musapembedze mulungu wina, pakuti Yehova amene dzina lake ndi Nsanje, ndi Mulungu wa nsanje. “Musamale kuti musakachite mgwirizano ndi anthu amene akukhala mʼdziko limene mukupitalo, chifukwa iwo akamakachita zadama ndi milungu yawo ndi kupereka nsembe, adzakuyitanani ndipo inu mudzadya nsembe zawo. Ndipo inu mukasankha ena mwa ana awo aakazi kukhala akazi a ana anu, akaziwo akakachita zadama ndi milungu yawo, akatsogolera ana anu aamuna kuchita chimodzimodzi. “Musadzipangire milungu yosungunula. “Muzichita chikondwerero cha buledi wopanda yisiti. Kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti monga momwe ndinakulamulirani. Muzichita zimenezi pa nthawi yoyikika mwezi wa Abibu, pakuti mwezi umenewu inu munatuluka mʼdziko la Igupto. “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga, pamodzi ndi ziweto zoyamba kubadwa zazimuna kuchokera ku ngʼombe kapena nkhosa. Muziwombola mwana woyamba kubadwa wa bulu popereka mwana wankhosa. Mukapanda kumuwombola mupheni. Muziwombola ana anu onse aamuna. “Palibe ndi mmodzi yemwe adzaonekere pamaso panga wopanda kanthu mʼdzanja lake. “Muzigwira ntchito masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri, musagwire ntchito ina iliyonse, Ngakhale nthawi yolima ndi yokolola muyenera kupuma. “Muzichita Chikondwerero cha Masabata, chifukwa ndi chikondwerero cha tirigu woyambirira kucha, ndiponso ndi chikondwerero cha kututa zokolola pakutha pa chaka. Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu wa Israeli, katatu pa chaka. Ine ndidzapirikitsa mitundu inayo pamene inu mukufikako ndi kukulitsa malire anu. Palibe ndi mmodzi yemwe adzafune kulanda dziko lanu ngati inu muzidzapita katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, chaka chilichonse. “Musapereke magazi anyama ngati nsembe kwa Ine pamodzi ndi chilichonse chimene chili ndi yisiti, ndipo musasunge nsembe ya pa Chikondwerero cha Paska mpaka mmawa. “Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.” Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba mawu awa pakuti potsatira mawuwa, ine ndipangana pangano ndi iwe ndi Israeli.” Mose anakhala kumeneko pamodzi ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku, wosadya kanthu kapena kumwa madzi. Ndipo iye analemba pa miyala ija mawu a pangano, malamulo khumi. Nkhope ya Mose Inyezimira Mose anatsika kuchokera mʼPhiri la Sinai pamodzi ndi miyala iwiri ija ya pangano mʼmanja mwake. Iye sanazindikire kuti nkhope yake imanyezimira pakuti anayankhula ndi Yehova. Aaroni ndi Aisraeli ataona kuti nkhope ya Mose imanyezimira anaopa kumuyandikira. Koma Mose anawayitana. Kotero Aaroni ndi atsogoleri onse a gululo anabwera kwa iye, ndipo anawayankhula. Kenaka Aisraeli onse anamuyandikira, ndipo anawapatsa malamulo onse omwe Yehova anamupatsa pa Phiri la Sinai. Mose atamaliza kuyankhula nawo anaphimba nkhope yake. Koma nthawi zonse popita pamaso pa Yehova kukayankhula naye amachotsa chophimbacho mpaka atatuluka. Ndipo akatuluka kudzawuza Aisraeli zimene walamulidwa, iwo amaona nkhope yake ikunyezimira. Choncho Mose amaphimba nkhope yake ngakhale pamene amapita kukayankhula ndi Yehova. Malamulo Osunga Sabata Mose anasonkhanitsa gulu lonse la Aisraeli ndipo anawawuza kuti, “Zinthu zimene Yehova wakulamulirani kuti muzichite ndi izi: Muzigwira ntchito zanu pa masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku la chisanu ndi chiwiri likhale la Sabata, tsiku lanu lopuma, lopatulika kwa Yehova. Aliyense amene adzagwira ntchito iliyonse pa tsikuli ayenera kuphedwa. Pa tsiku la Sabata musakoleze moto paliponse pamene mukhala.” Zopereka ku Malo Opatulika Mose ananena kwa gulu lonse la Aisraeli kuti, “Zimene Yehova wakulamulirani ndi izi: Kuchokera pa zomwe muli nazo, mutenge chopereka cha Yehova. Aliyense amene ali ndi mtima wofuna kupereka abweretse kwa Yehova zopereka izi: Golide, siliva ndi mkuwa; nsalu zobiriwira, zapepo, zofiira, nsalu zofewa; ubweya wambuzi; zikopa za nkhosa zazimuna za utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu; matabwa amtengo wa mkesha, mafuta anyale a olivi, zonunkhiritsa mafuta odzozera ndi zopangira lubani wonunkhira; miyala yokongola ya mtundu wa onikisi ndi ina yabwino yoyika pa Efodi ndi pa chovala cha pachifuwa. “Anthu onse aluso pakati panu abwere ndi kupanga zonse zimene Yehova walamula: Chihema ndi tenti yake ndiponso chophimba chake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; Bokosi la Chipangano pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake cha bokosilo ndi nsalu zophimba bokosilo; tebulo pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira pamodzi ndi zipangizo zake zonse ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; choyikapo nyale yowunikira pamodzi ndi zipangizo zake, nyale ndi mafuta anyalezo; guwa lofukizira lubani pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira, mafuta odzozera ndi lubani onunkhira; nsalu yotchinga pa khomo lolowera mʼchihema; guwa lansembe yopsereza pamodzi ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse, beseni losambira lamkuwa ndi miyendo yake; nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake, ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zikhomo za tenti ya chihema ndiponso za bwalo, ndi zingwe zake; zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe.” Kenaka gulu lonse la Aisraeli linachoka pamaso pa Mose, ndipo aliyense amene anakhudzidwa mu mtima mwake nafuna kupereka, anabwera kudzapereka chopereka kwa Yehova cha ntchito yokonza tenti ya msonkhano, cha ntchito zonse za mʼtentimo ndi cha zovala zopatulika. Onse amene anali ndi mtima wofuna, amuna ndi amayi omwe anabwera kudzapereka zodzikometsera zagolide za mtundu uliwonse: zomangira zovala, ndolo, mphete ndi zokometsera. Onse anapereka golide wawo monga nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. Aliyense amene anali ndi nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo kapena yofiira kapena yofewa, yosalala, kapena ubweya wambuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira kapena zikopa anazibweretsa. Onse amene anapereka chopereka cha siliva kapena mkuwa anabweretsa monga chopereka kwa Yehova. Ndipo aliyense amene anali ndi matabwa a mtengo wa mkesha kuti awagwiritse ntchito mbali ina iliyonse ya ntchitoyo, anabweretsa. Mayi aliyense waluso analuka ndi manja ake ndi kubweretsa chomwe analuka cha mtundu wa mtambo, chapepo kapena chofiira kapena chofewa, chosalala. Ndipo amayi onse amene anali ndi mtima wofuna ndipo anali ndi luso analuka ubweya wa mbuzi. Atsogoleri anabweretsa miyala ya onikisi ndi miyala yokongola yoyika pa efodi ndi chovala chapachifuwa. Anabweretsanso zonunkhiritsa ndiponso mafuta owunikira a olivi ndi odzozera ndi zofukizira zonunkhira. Aisraeli onse aamuna ndi aakazi amene anali ndi mtima wofuna, anabweretsa kwa Yehova chopereka chaufulu ku ntchito yonse ya Yehova imene analamulira kudzera mwa Mose kuti achite. Bezaleli ndi Oholiabu Kenaka Mose anati kwa Aisraeli, “Taonani, Yehova wasankha Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri, wa fuko la Yuda, ndipo wamudzaza ndi Mzimu wa Mulungu kotero kuti ali ndi luso ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndipo akudziwa bwino ntchito zonse zamanja monga izi: Kulemba ndondomeko ya ntchito zaluso ndi kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa, kusema ndi kuyika miyala yokongola, kukonza zinthu zamatabwa ndiponso kugwira ntchito ina iliyonse yamanja. Ndipo Iye wapereka kwa Bezaleli pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani luso lophunzitsa ena. Mulungu wawapatsa maluso osiyanasiyana, maluso ogoba, olemba ndondomeko, opeta zokometsera pa nsalu zamtundu wamtambo, zapepo ndi zofiira ndiponso zofewa zosalala ndi zoluka. Onsewa ndi amisiri a ntchito zamanja ndi zokonza ndondomeko. Choncho Bezaleli, Oholiabu pamodzi ndi anthu aluso onse amene Yehova anawapatsa luso ndi nzeru zodziwira kupanga zofunika zonse zomangira malo opatulika, adzapanga zonse iwowo, monga momwe Yehova analamulira.” Ndipo Mose anayitana Bezaleli ndi Oholiabu ndiponso munthu aliyense waluso amene Yehova anamupatsa luso ndiponso amene anali ndi mtima wofuna kugwira ntchito. Iwo analandira kuchokera kwa Mose zopereka zonse Aisraeli anabweretsa kuti agwirire ntchito yomanga malo wopatulika. Ndipo anthu anapitirira kupereka zopereka zaufulu mmawa uliwonse. Kotero amisiri onse amene amagwira ntchito yonse ya malo wopatulika anasiya ntchitoyo ndipo anati kwa Mose, “Anthu akubweretsa kuposa zimene zikufunika kugwirira ntchito imene Yehova analamulira kuti ichitike.” Choncho Mose analamulira ndipo analengeza mu msasa onse, “Mwamuna kapena mayi aliyense asaperekenso chopereka chilichonse cha ku malo wopatulika.” Choncho anthu analetsedwa kubweretsa zambiri, chifukwa zimene anali nazo zinali zoposera zimene zimafunika kugwirira ntchito yonse. Chihema Anthu onse aluso pakati pa anthu ogwira ntchitoyo anapanga chihema pogwiritsa ntchito nsalu khumi zofewa, zosalala ndi zolukidwa bwino, zobiriwira, zapepo ndi zofiira. Ndipo anthu aluso anapeta pa nsaluzo Akerubi. Nsalu zonse zinali zofanana. Mulitali mwake zinali mamita khumi ndi atatu, mulifupi mamita awiri. Iwo analumikiza nsalu zisanu, kuti ikhale nsalu imodzi ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu zisanu zinazo. Kenaka anapanga zokolowekamo za nsalu yobiriwira mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsiriza ya mbali ina. Ndipo anachita chimodzimodzi ndi nsalu yotsiriza ya mbali inayo. Iwo anasokerera zokolowekamo makumi asanu pa nsalu yoyamba ndi zokolowekamo makumi asanu zinanso pa nsalu inayo. Anapanga kuti zokolowekamozo ziziyangʼanana. Kenaka anapanga ngowe zagolide 50 zolumikizira nsalu ziwirizo kotero kuti zinapanga chihema chimodzi. Iwo anapanga nsalu za ubweya wambuzi zophimba pamwamba pa chihemacho. Nsalu zonse pamodzi zinalipo khumi ndi imodzi. Nsalu zonse khumi ndi imodzi zinali zofanana. Mulitali mwake munali mamita khumi ndi anayi ndipo mulifupi mwake munali mamita awiri. Iwo analumikiza nsalu zisanu kukhala nsalu imodzi ndipo nsalu zinazo zisanu ndi imodzi, analumikizanso kukhala nsalu imodzinso. Kenaka anasokerera zokolowekamo makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu imodzi yotsirizira ya nsalu yoyamba yolumikiza ija ndiponso anapanga zokolowekamo zina makumi asanu mʼmphepete mwa nsalu yotsirizira ya nsalu inanso yolumikiza ija. Iwo anapanga ngowe 50 zamkuwa zolowetsa mu zokolowekazo ndipo anaphatikiza nsalu ziwirizo kuti tentiyo ikhale imodzi. Ndipo anapanga chikopa cha nkhosa zazimuna cha utoto wofiira chophimbira tentiyo ndipo pamwamba pake anapanganso chophimbira china cha zikopa za akatumbu. Iwo anapanga maferemu amatabwa amtengo wa mkesha oyimikira chihemacho. Feremu iliyonse inali yotalika mamita anayi ndipo mulifupi mwake munali masentimita 69. Thabwa lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri. Iwo anapanga maferemu onse a chihemacho ndi matabwa otere. Anapanga maferemu makumi awiri a mbali yakummwera kwa chihemacho, ndiponso anapanga matsinde 40 asiliva ndipo anawayika pansi pa maferemuwo. Pansi pa feremu iliyonse anayika matsinde awiri ogwiriziza zolumikizira ziwiri zija. Iwo anapanganso maferemu makumi awiri a mbali yakumpoto ya chihemacho, ndiponso matsinde makumi anayi asiliva, awiri pansi pa feremu iliyonse. Anapanganso maferemu asanu ndi imodzi a kumbuyo kwa tenti, kumbali yakumadzulo, ndiponso maferemu awiri a pa ngodya yakumbuyo kwenikweni kwa tenti. Pa ngodya ziwirizi panali maferemu awiri, kuyambira pansi mpaka pamwamba atalumikizidwa pa ngowe imodzi. Maferemu onse anali ofanana. Choncho panali maferemu asanu ndi atatu ndiponso matsinde 16 asiliva, awiri anali pansi pa feremu iliyonse. Iwo anapanganso mitanda ya matabwa amtengo wa mkesha. Mitanda isanu inali ya maferemu a mbali imodzi ya chihema, mitanda isanu inanso inali ya maferemu a mbali inayo ndipo mitanda ina isanu ya mbali yakumadzulo, kumapeto kwenikweni kwa chihema. Anapanga mtanda wapakati omwe umachokera pa maferemu a mbali ina mpaka mbali inanso. Iwo anakuta maferemuwo ndi golide ndiponso anapanga mphete zagolide zogwiriziza mitandayo. Ndipo mitandayonso anayikuta ndi golide. Anapanga nsalu yokhala ndi mtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira ndipo nsaluyo inali yolukidwa bwino, yofewa ndi yosalala. Ndipo anthu aluso anapetapo zithunzi za Akerubi. Iwo anapanga nsanamira zinayi zamtengo wa mkesha zokutidwa ndi golide. Anapanganso ngowe zagolide za nsanamirazo ndi matsinde asiliva anayi. Anapanga nsalu ya pa chipata cholowera mu chihema, yamtundu wamtambo, wapepo ndi ofiira yomwe inali yofewa ndi yosalala, yopetedwa bwino ndi amisiri aluso. Anapanga nsanamira zisanu ndi ngowe zake. Anakuta pamwamba pa nsanamirazo ndi zomangira zake ndi golide, ndipo anapanganso matsinde asanu amkuwa. Bokosi la Chipangano Bezaleli anapanga Bokosi la Chipangano lamatabwa amtengo wa mkesha. Kutalika kwake kunali masentimita 114, mulifupi mwake munali masentimita 69, msinkhu wake masentimita 69. Iye analikuta bokosilo ndi golide wabwino kwambiri mʼkati mwake ndi kunja komwe. Anapanganso mkombero wagolide kuzungulira bokosilo. Iye anapanga mphete zinayi zagolide ndi kuzimangirira ku miyendo yake inayi ija, mbali ina ziwiri ndi mbali inanso ziwiri. Kenaka anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide. Ndipo analowetsa nsichizo mʼmphete zija za mbali zonse ziwiri za bokosilo kuti azinyamulira. Iye anapanga chivundikiro cha bokosilo cha golide wabwino kwambiri, kutalika kwake masentimita 114, mulifupi mwake masentimita 69. Ndipo anapanga Akerubi awiri agolide osula ndi nyundo ndi kuwayika mbali ziwiri za chivundikirocho. Iye anapanga kerubi mmodzi mbali ina ndi wina mbali inayo. Akerubiwa anawapangira limodzi ndi chivundikirocho mʼmapeto mwa mbali ziwirizo. Mapiko a Akerubiwo anatambasukira pamwamba pa chivundikiro cha bokosilo kuti achiphimbe. Akerubiwo anakhala choyangʼanana, aliyense kuyangʼana chivundikirocho. Mapangidwe a Tebulo Iwo anapanga tebulo la matabwa amtengo wa mkesha, mulitali mwake masentimita 91, mulifupi mwake masentimita 46, msinkhu wake masentimita 69. Kenaka analikuta ndi golide wabwino kwambiri, ndipo anapanga mkombero wagolide mʼmbali mwake. Iwo anapanga feremu yozungulira tebulo, mulifupi mwake ngati chikhatho cha dzanja, ndipo anayika mkombero wagolide kuzungulira feremuyo. Iwo anapanga mphete zinayi zagolide ndipo anazilumikiza ku ngodya zake zinayi, kumene kunali miyendo yake inayi. Mphetezo anaziyika kufupi ndi feremu kuti azikolowekamo nsichi zonyamulira tebuloyo. Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndi kuzikuta ndi golide kuti azinyamulira tebulolo. Ndipo anapanga ziwiya za pa tebulolo zagolide wabwino, mbale ndi zipande, mitsuko ndi mabeseni zogwiritsa ntchito popereka nsembe za chakumwa. Mapangidwe a Choyikapo Nyale Iwo anapanga choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri. Tsinde lake ndi mphanda zake zinasulidwa ndi nyundo. Zikho zake zokhala ndi mphukira ndi maluwa ake zinapangidwa kumodzi. Mʼmbali mwake munali mphanda zisanu ndi imodzi, zitatu mbali iliyonse. Zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa zinali pa mphanda yoyamba. Pa mphanda yachiwiri panalinso zikho zitatu zokhala ngati za maluwa amtowo, mphukira ndi duwa. Ndipo mphanda zonse zisanu ndi imodzi zinali chimodzimodzi ndipo zinatuluka mʼchoyikapo nyalecho. Pa choyikapo nyalecho panali zikho zinayi zokhala ngati maluwa amtowo, mphukira ndi maluwa ake. Mphukira yoyamba inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zoyamba za pa choyikapo nyale. Mphukira yachiwiri inali mʼmunsi mwa nthambi ziwiri zinazo. Mphukira yachitatu inali mʼmunsi mwa nthambi zina ziwirinso. Zonse pamodzi zinali nthambi zisanu ndi imodzi Mphukira ndi nthambi zonse zinasulidwa kumodzi ndi choyikapo nyalecho ndi golide wabwino kwambiri. Iwo anapanga nyale zisanu ndi ziwiri, mbaniro ndi zowolera phulusa, zonse zinali zagolide wabwino kwambiri. Iwo anapanga choyikapo nyale ndi zipangizo zake zonse zagolide wabwino kwambiri wolemera makilogalamu 34. Guwa Lofukizirapo Lubani Iwo anapanga guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. Linali lofanana mbali zonse, mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91, ndipo nyanga zake zinapangidwa kumodzi ndi guwalo. Iwo anakuta guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse ndi nyanga zake, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwalo. Anapanga mphete ziwiri pansi pa mkomberowo ndi kulumikiza ku mbali zonse ziwiri kuti apisemo nsichi zonyamulira. Anapanga mizati yamtengo wa mkesha ndipo anayikuta ndi golide. Iwo anapanganso mafuta opatulika odzozera ndi zofukiza za fungo lokoma kwambiri. Iyi inali ntchito ya mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Guwa Lansembe Yopsereza Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229. Anapanga nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo, kotero kuti nyangazo ndi guwalo zinali chinthu chimodzi, ndipo anakuta guwalo ndi mkuwa. Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo. Anapanga mphete zamkuwa zinayi ndipo anazilumikiza ku ngodya zinayi za sefa ija kuti zigwire nsichi zonyamulira. Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndipo anazikuta ndi mkuwa. Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake. Beseni Losambira Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano. Bwalo la Chihema Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. Anapanganso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. Mbali yakumadzulo inali yotalika mamita 23 ndipo inali ndi nsalu yotchinga, mizati khumi ndi matsinde khumi. Inalinso ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, inalinso yotalika mamita 23. Mbali imodzi yachipata kunali nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu, polowera mʼbwalo panali nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu. Katani yonse yotchinga kuzungulira chihema inali yofewa, yosalala ndi yolukidwa bwino. Matsinde amizati anali amkuwa. Ngowe ndi zingwe za mizati zinali zasiliva, ndipo pamwamba pa mizatiyo anakutapo siliva. Choncho mizati yonse ya bwalolo inalumikizidwa ndi zingwe zasiliva. Nsalu yotchinga ya pa chipata inali yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira, yofewa yosalala ndi yopangidwa ndi anthu aluso. Nsaluyo inali yotalika mamita asanu ndi anayi, molingana ndi nsalu zotchinga bwalo. Msinkhu wake unali masentimita 229, pamodzi ndi mizati yake inayi ndi matsinde amkuwa anayi. Ngowe ndi zingwe zake zinali za siliva, ndipo pamwamba pake pa mzati anakutapo ndi siliva. Zikhomo za chihema ndi zina zonse zozungulira chihemacho zinali zamkuwa. Zipangizo Zachitsulo za ku Malo Opatulika Chiwerengero cha zipangizo zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, chihema chaumboni, zimene Mose analamulira Alevi kuti alembe motsogozedwa ndi Itamara mwana wa Aaroni, wansembe, chinali ichi: Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huzi wa fuko la Yuda anapanga chilichonse Yehova analamulira Mose, pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, wa luso la zopangapanga ndi kulemba mapulani, ndi wopanga nsalu zolukidwa bwino za mtundu wa mtambo, yapepo ndi zofiira, zofewa ndi zosalala. Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika. Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika. Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550. Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi. Makilogalamu otsalawo anagwiritsa ntchito popanga ngowe zamzati kukutira pamwamba pa mizati ndiponso kupanga zingwe zake. Mkuwa ochokera ku nsembe yoweyula unali makilogalamu 2,425. Iwo anawugwiritsa ntchito popanga matsinde a pa chipata cha tenti ya msonkhano, guwa la mkuwa pamodzi ndi sefa yake ndiponso ziwiya zonse, matsinde ozungulira bwalo ndiponso a pa chipata pake, ndi zikhomo zonse za tentiyo ndi matsinde a malo wozungulirapo. Zovala za Ansembe Anapanga zovala za ansembe, zovala potumikira ku malo wopatulika pogwiritsa ntchito nsalu ya mtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira. Anapanganso zovala zopatulika za Aaroni monga momwe Yehova analamulira Mose. Chovala cha Efodi Popanga efodi, iwo anagwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yosalala yofewa. Anasula golide wopyapyala ndi kumulezaleza kuti alumikize kumodzi ndi nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yosalala yofewa yolukidwa mwaluso. Iwo anapanga efodi imene inali ndi timalamba tiwiri ta pa mapewa, tosokerera ku msonga zake ziwiri kuti azitha kumanga. Lamba womangira efodi anali wolukidwa mwaluso ngati efodiyo. Anali nsalu imodzi ndi efodiyo, wopangidwa ndi golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala, monga momwe Yehova analamulira Mose. Iwo anakonza miyala ya onikisi ndi kuyiika mu zoyikamo zake zagolide ndipo anazokota mayina a ana a Israeli monga amachitira pa chidindo. Kenaka anayimangirira pa tinsalu ta mʼmapewa ta efodi tija ngati miyala ya chikumbutso cha ana a Israeli monga momwe Yehova analamulira Mose. Chovala Chapachifuwa Iwo anapanga chovala chapachifuwa mwaluso kwambiri. Anachipanga ngati efodi pogwiritsa ntchito golide, nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo, yofiira, yofewa yosalala ndi yolukidwa bwino. Kutalika kwake kunali kofanana mbali zonse, mulitali masentimita 23, mulifupi masentimita 23, chinali chopinda pawiri. Kenaka anayikapo mizere inayi ya miyala yokongola kwambiri. Mzere woyamba anayika miyala ya rubi, topazi ndi berili; mzere wachiwiri anayikapo miyala ya emeradi, safiro ndi dayimondi; mzere wachitatu anayikapo miyala ya opera, agate ndi ametisiti; mzere wachinayi anayikapo miyala ya topazi, onikisi ndi yasipa. Miyalayi anayiyika mu zoyikamo zagolide. Miyalayo inalipo khumi ndi iwiri, uliwonse kuyimira dzina limodzi la ana a Israeli. Mwala uliwonse unazokotedwa ngati chidindo dzina limodzi la mafuko khumi ndi awiri a Israeli. Anapanga timaunyolo tagolide wabwino kwambiri ta pa chovala chapachifuwa, topota ngati chingwe. Anapanganso zoyikamo zake zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anamangirira mphetezo pa ngodya ziwiri za chovala chapachifuwa. Anamangirira timaunyolo tiwiri tagolide tija pa mphete za pa ngodya pa chovala chapachifuwacho. Ndipo mbali ina ya timaunyoloto anamangirira pa zoyikapo zake ziwiri zija, ndi kulumikiza pa tinsalu takutsogolo kwa mapewa a efodi. Anapanganso mphete ziwiri zagolide ndipo analumikiza ku ngodya ziwiri zamʼmunsi mwa chovala chapachifuwa, champhepete mwake, mʼkati pafupi ndi efodi ija. Kenaka anapanga mphete zina ziwiri zagolide ndi kuzilumikiza kumunsi kwa tinsalu takutsogolo kwa efodi, pafupi ndi msoko, pamwamba pangʼono pa lamba wamʼchiwuno wa efodi. Anamangirira mphete za pa chovala chapachifuwa zija ku mphete za efodi ndi chingwe chamtundu wa mtambo, kulumikiza lamba ndi chovala chapachifuwacho kuti chovala chapachifuwacho chisalekane ndi efodi ija monga Yehova analamulira Mose. Zovala zina za Unsembe Anayipangira efodiyo mkanjo wamtundu wa mtambo, wolukidwa ndi mmisiri waluso. Mkanjowo unali ndi malo opisapo mutu pakati pakepo. Pa chibowopo panali chibandi chosokedwa mochita ngati kuluka monga muja akhalira malaya kuti chibowocho chilimbe, chisangʼambike. Pa mpendero wamʼmunsi wa mkanjowo, analumikiza mphonje zokhala ngati makangadza za nsalu yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira yofewa yosalala ndi yopetedwa bwino yomwe inazungulira mkanjo. Ndipo anapanga maberu agolide wabwino kwambiri ndipo analumikiza mozungulira mpendero pakati pa makangadzawo. Kotero panali mphonje imodzi ndi belu limodzi kuzungulira mpendero wa mkanjo wovala potumikira monga momwe Yehova analamulira Mose. Kwa Aaroni ndi ana ake anawapangira minjiro ya nsalu yofewa yosalala, yolukidwa bwino ndi munthu waluso, nduwira ya nsalu yofewa yosalala, lamba wa nsalu yofewa yosalala, womanga mʼmutu, ndi makabudula amʼkati a nsalu yofewa yosalala olukidwa bwino. Anapanga lamba wolukidwa bwino wa nsalu yofewa ndi yosalala ya mtundu wa mtambo yapepo ndi yofiira. Ili linaliluso la munthu wopanga zokometsera monga Yehova analamulira Mose. Iwo anapanga duwa lagolide wabwino kwambiri ngati chidindo ndipo anazokotapo mawu akuti, Wopatulikira Yehova. Kenaka analimangira ndi chingwe cha nsalu yamtundu wa mtambo pa nduwira, monga momwe Yehova analamulira Mose. Mose Ayendera Chihema Tsopano ntchito yonse ya tenti ya msonkhano inatha. Aisraeli anachita zonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Kenaka anabweretsa chihema kwa Mose. Tenti ndi zipangizo zake, ngowe zake, maferemu ake, mitanda yake, mizati yake ndi matsinde ake; chophimba cha chikopa cha nkhosa yayimuna chonyikidwa mu utoto ofiira, chophimba cha chikopa cha akatumbu ndi nsalu zophimba; bokosi la umboni pamodzi ndi mitengo yake yonyamulira ndiponso chovundikira chake; tebulo pamodzi ndi zipangizo zake ndiponso buledi wokhala pamaso pa Yehova; choyikapo nyale chagolide wabwino kwambiri pamodzi ndi nyale zake ndi zipangizo zake zonse, ndiponso mafuta anyalezo; guwa lagolide, mafuta odzozera, lubani onunkhira ndi nsalu yotchinga pa khomo lolowera mu tenti; guwa lamkuwa ndi sefa yamkuwa, mitengo yake yonyamulira ndi zipangizo zake zonse; beseni ndi miyendo yake; nsalu yotchingira bwalo pamodzi ndi mizati yake ndi matsinde ake ndiponso nsalu yotchingira pa khomo lolowera ku bwalo; zingwe zake ndi zikhomo za tenti; zipangizo zonse za chihema, tenti ya msonkhano; ndiponso zovala zolukidwa zovala potumikira kumalo opatulika, zovala zopatulika za wansembe, Aaroni pamodzi ndi za ana ake aamuna pamene akutumikira monga ansembe. Aisraeli anagwira ntchito yonse monga momwe Yehova analamulira Mose. Mose anayendera ntchitoyo ndipo anaona kuti anayichita monga momwe Yehova analamulira. Kotero Mose anawadalitsa. Adzutsa Chihema Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Imika chihema, tenti ya msonkhano, tsiku loyamba la mwezi. Uyikemo bokosi la umboni ndipo uphimbe bokosilo ndi katani. Ulowetsemo tebulo ndi kuyika zimene zimakhala pamenepo. Kenaka ulowetse choyikapo nyale ndipo uyikepo nyale zake. Uyike guwa lofukiza la golide patsogolo pa bokosi la umboni ndipo uyike katani ya pa chipata cha chihema. “Uyike guwa lansembe yopsereza patsogolo pa chipata cha chihema, tenti ya msonkhano. Uyike beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uyikemo madzi. Upange bwalo lozungulira chihemacho ndipo uyike katani ya pa chipata cha bwalolo. “Utenge mafuta wodzozera ndipo udzoze chihema ndi chilichonse chili mʼmenemo ndipo zidzakhala zoyeretsedwa. Kenaka udzoze guwa lansembe lopsereza ndi ziwiya zake zonse. Ulipatule guwalo ndipo lidzakhala loyera kwambiri. Udzoze beseni ndi miyendo yake ndipo uzipatule. “Ubwere ndi Aaroni ndi ana ake pa chipata cha tenti ya msonkhano ndipo uwasambitse ndi madzi. Kenaka umuveke Aaroni zovala zopatulika, umudzoze ndi kumupatula kotero kuti athe kunditumikira monga wansembe. Ubweretse ana ake ndipo uwaveke minjiro. Uwadzoze monga momwe unadzozera abambo awo, kotero kuti anditumikire monga ansembe. Kudzozedwako kudzakhala unsembe wawo pa mibado ndi mibado” Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira. Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri. Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi. Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose. Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake. Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye. Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani, ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose. Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema. Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose. Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira. Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema. Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira. Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba, ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo. Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose. Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito. Ulemerero wa Yehova Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo. Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke. Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.