- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 ESTERE Estere Estere Est Estere Vasiti Mkazi wa Mfumu Achotsedwa Izi ndi zimene zinachitika pa nthawi ya ufumu wa Ahasiwero, amene analamulira zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Pa nthawi imeneyi nʼkuti mfumu Ahasiwero atakhazikika pa mpando wake wa ufumu mu mzinda wa Susa, ndipo mʼchaka chachitatu cha ufumu wake anakonza phwando la olemekezeka ndi nduna zake. Atsogoleri a nkhondo a ku Peresiya ndi Mediya, anthu olemekezeka pamodzi ndi nduna za mʼzigawo zonse anasonkhana kwa iye. Pa nthawi yomweyi kwa masiku 180 a phwando mfumu inkaonetsa kulemera kwa ulemerero wa ufumu wake ndiponso kukongola ndi kukula kwa ufumu wake. Atatha masiku amenewa, kwa masiku ena asanu ndi awiri mfumu inakonzanso phwando la anthu onse okhala mu mzinda wa Susa kuyambira anthu olemekezeka mpaka anthu wamba ku bwalo la munda la nyumba yake yaufumu. Bwalo la mundali analikongoletsa ndi makatani a nsalu zoyera ndi za mtundu wamtambo zimene anazimangirira ndi zingwe za nsalu zoyera ndi zapepo ku mphete za siliva zimene anazikoloweka pa nsanamira za maburo. Anayika mipando yopumirapo yagolide ndi siliva pabwalo la miyala yoyala yamtengowapatali yofiira, ya marabulo, ndi yonyezimira. Anapereka zakumwa mʼchikho zagolide zamitundumitundu, ndipo vinyo waufumu anali wochuluka kwambiri monga mwa kukoma mtima kwa mfumu. Monga mwa lamulo la mfumu aliyense anamwa mʼmene anafunira, pakuti mfumu inawuza otumikira ake kuti apatse aliyense monga mwa kukonda kwake. Mkazi wa mfumu Vasiti nayenso anakonzera phwando amayi ku nyumba ya ufumu ya mfumu Ahasiwero. Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri, pamene mfumu Ahasiwero inaledzera ndi vinyo, inalamula adindo ofulidwa asanu ndi awiri amene ankamutumikira: Mehumani, Bizita, Haribona, Bigita, Abagita, Zetara, ndi Karikasi kuti abwere naye mfumukazi Vasiti pamaso pa mfumu atavala chipewa chaufumu. Cholinga cha mfumu chinali choti adzamuonetse kwa anthu onse ndi olemekezeka, chifukwa anali wokongola kwambiri. Koma antchito atapereka uthenga wa mfumu kwa mfumukazi, Vasiti anakana kubwera. Tsono mfumu inakwiya ndi kupsa mtima. Mfumu inayankhula ndi anthu anzeru ndi ozindikira choyenera kuchita popeza chinali chikhalidwe chake kufunsa uphungu kwa akatswiri pa nkhani za malamulo ndi kuweruza kolungama. Anthu amene ankakhala pafupi ndi mfumu anali awa: Karisena, Setara, Adimata, Tarisisi, Meresi, Marisena ndi Memukani, olemekezeka asanu ndi awiri a ku Peresiya ndi Medina amene ankaloledwa mwapadera kuonana ndi mfumu ndipo anali pamwamba kwambiri mu ufumuwo. Mfumu inafunsa kuti, “Kodi titani naye mfumukazi Vasiti mwa lamulo, popeza sanamvere lamulo la ine mfumu Ahasiwero limene adindo ofulidwa anakamuwuza?” Ndipo Memukani anayankha pa maso pa mfumu ndi olemekezeka anzake kuti, “Mfumukazi Vasiti sanalakwire mfumu yokha, koma walakwiranso olemekezeka onse ndi anthu onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero. Pakuti amayi onse adzadziwa zimene wachita mfumukazi ndipo kotero adzapeputsa amuna awo ndi kunena kuti, ‘Mfumu Ahasiwero analamulira kuti abwere naye mfumukazi Vasiti kwa iye koma sanapite.’ Lero lomwe lino amayi olemekezeka a ku Peresiya ndi Mediya amene amva zimene wachita mfumukazi adzaganiza zochita chimodzimodzi kwa nduna zonse za mfumu. Ndipo kupeputsana ndi kukongola zidzapitirira.” “Choncho, ngati chikukomerani mfumu, lamulirani kuti Vasiti asadzaonekerenso pamaso pa mfumu Ahasiwero. Lamuloli lilembedwe mʼmabuku a malamulo a Aperezi ndi Amedi kuti lisadzasinthike. Pamalo pa Vasiti ngati mfumukazi payikidwepo mkazi wina amene ali bwino kuposa iye. Ndipo lamulo la mfumuli lilengezedwa mʼdziko lake lonse ngakhale lili lalikulu, amayi onse adzapereka ulemu kwa amuna awo, amuna olemekezeka mpaka amuna wamba.” Mfumu ndi nduna zake anakondwera ndi uphungu uwu, kotero mfumu inachita monga momwe ananenera Memukani. Mfumu inatumiza makalata ku madera onse a ufumu wake, chigawo chilichonse mʼzilembo zawo ndi ku mtundu uliwonse mʼchiyankhulo chawochawo kulengeza kuti mwamuna ayankhule chilichonse chimene chikumukomera. Mfumu Ikwatira Estere Pambuyo pake mtima wa Ahasiwero utatsika, Ahasiwero anakumbukira Vasiti ndi zimene anachita Vasitiyo. Anakumbukiranso lamulo lomukhudza limene anasindikiza. Tsono anyamata a mfumu amene ankamutumikira anati, “Mfumu, akufunireni anamwali okongola. Mfumu isankhe oyangʼanira pa chigawo chilichonse cha ufumu wake kuti abwere nawo pamodzi anamwali onse okongola ku nyumba yosungira akazi ku Susa. Hegai, mdindo wofulidwa wa mfumu, amene amayangʼanira amayi, akhale wosamalira anamwaliwa ndipo aziwapatsa mafuta odzola. Ndipo namwali amene mfumu yakondwera naye akhale mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti.” Mfumu inakondwera ndi uphunguwu, ndipo inachita momwemo. Myuda wina wa fuko la Benjamini, dzina lake Mordekai, mwana wa Yairi, mwana wa Simei, mwana wa Kisi, anali mu mzinda wa Susa. Iyeyu anali mmodzi mwa anthu amene anatengedwa ukapolo ndi Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu pamodzi ndi Yekoniya mfumu ya Yuda. Mordekai nʼkuti atalera Hadasa, amene ankatchedwanso Estere, mwana wamkazi wa amalume ake chifukwa analibe abambo kapena amayi. Mtsikanayu anali wokongola ndi wooneka bwino ndipo Mordekai ankamutenga ngati mwana wake weniweni pamene abambo ndi amayi ake anamwalira. Lamulo la mfumu atalilengeza ndi kubwera nawo pamodzi anamwali ambiri ku mzinda wa Susa kuti akasamalidwe ndi Hegai, Estere nayenso anatengedwa kupita naye ku nyumba ya mfumu kuti akasamalidwe ndi Hegai woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi uja. Hegai anasangalatsidwa naye namwaliyo ndipo anamukomera mtima. Mosataya nthawi anamupatsa mafuta ake odzola ndi chakudya chapadera. Anamusankhiranso anamwali asanu ndi awiri a ku nyumba ya mfumu kuti azimutumikira, ndipo iye pamodzi ndi anamwali omutumikira aja anawapatsa malo abwino koposa mʼnyumba yosungira akazi. Estere sanawulule mtundu wake ndi abale ake chifukwa Mordekai anamuletsa kutero. Tsiku ndi tsiku Mordekai ankayendayenda pafupi ndi bwalo la nyumba yosungiramo akazi ija kuti adziwe za moyo wa Estere ndi kuti zinthu zikumuyendera bwanji. Tsono nthawi inkafika kuti namwali aliyense akaonekere kwa mfumu Ahasiwero, pakutha pa miyezi khumi ndi iwiri yomwe inakhazikitsidwa kuti amayi azidzikongoletsa. Pa miyezi isanu ndi umodzi ankadzola mafuta a mure ndipo pa miyezi isanu ndi umodzi inayo ankadzola zonunkhira ndi zokongoletsa. Ndipo namwali ankapita kwa mfumu motere: Ankaloledwa kutenga chilichonse angafune mʼnyumba yosungiramo akazi kupita nacho ku nyumba ya mfumu. Ankalowa madzulo kwa mfumu ndi kutuluka mmawa kupita ku nyumba ina yosungira akazi yomwe ankayangʼanira ndi Saasigazi, mdindo wofulidwa wa mfumu amene amayangʼanira akazi a mfumu. Namwali sankabwerera kwa mfumu pokhapokha amukomere mtima ndi kumuyitana potchula dzina lake. Tsono inafika nthawi kuti Estere, mwana wamkazi wa Abihaili amenenso analeredwa ndi Mordekai amalume ake, alowe kwa mfumu. Iye sanapemphe kanthu kalikonse, koma anatenga zokhazo zimene ananena Hegai mdindo wofulidwa wa mfumu woyangʼanira nyumba yosungiramo akazi. Ndipo aliyense amene anamuona Estere, anasangalatsidwa naye. Anapita naye kwa mfumu Ahasiwero ku nyumba ya ufumu pa mwezi wa khumi, mwezi wa Tebete, chaka cha chisanu ndi chiwiri cha ufumu wake. Ndipo mfumu inamukonda Estere koposa wina aliyense wa akazi aja, kotero inamukonda ndi kumukomera mtima koposa wina aliyense wa anamwali aja. Choncho anamumveka chipewa chaufumu pa mutu pake nakhala mfumukazi mʼmalo mwa Vasiti. Ndipo mfumu inakonza phwando lalikulu, phwando la Estere, kukonzera anthu olemekezeka ndi nduna zake zonse. Analamuliranso kuti anthu mʼzigawo zonse asapereke msonkho ndipo anapereka mphatso monga mwakukoma mtima kwa mfumu. Mordekai Awulula Chiwembu Anamwali atasonkhanitsidwa pamodzi, Mordekai anakhala pansi pa chipata cha mfumu. Koma Estere anali asanawululebe za mtundu wake ndi anthu a pa banja lake monga momwe analamulira Mordekai, chifukwa anapitirira kutsata malangizo a Mordekai monga ankachitira pamene ankamulera. Pa nthawi imene Mordekai ankalondera pa chipata cha mfumu, Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa amfumu, olondera pa khomo la nyumba yake, anayipidwa mtima ndipo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. Koma Mordekai atazindikira za chiwembuchi anawuza mfumukazi Estere ndipo iye anakawuza mfumu mʼmalo mwa Mordekai. Ndipo pamene anafufuza za chiwembuchi kuti zinali zoona, adindo awiriwa anaphedwa monyongedwa. Zinthu izi zinalembedwa mʼbuku la Mbiri ndi kusungidwa ndi Mfumu. Chiwembu cha Hamani Chopha a Yuda Zitachitika izi, mfumu Ahasiwero anamukweza Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, anamulemekeza ndikumupatsa mpando wa ulemu kuposa nduna zina zonse. Atumiki onse a mfumu amene anali pa chipata cha nyumba ya mfumu ankagwadira ndi kuweramira Hamani monga mwa lamulo la mfumu. Koma Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira. Kenaka atumiki a mfumu amene anali pa chipata anafunsa Mordekai kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani sumvera lamulo la mfumu?” Tsiku ndi tsiku ankayankhula naye koma iye sanamverebe. Choncho anamuwuza Hamani kuti aone ngati angavomereze khalidwe lotere la Mordekai, popeza anawawuza kuti anali Myuda. Hamani ataona kuti Mordekai sankamugwadira kapena kumuweramira, anapsa mtima kwambiri. Hamani atamva kuti Mordekai anali Myuda, anatsimikiza kuti ndi kosakwanira kulanga Mordekai yekha. Mʼmalo mwake anapeza njira yowonongera Ayuda onse okhala mʼdziko lonse limene mfumu Ahasiwero ankalamulira. Mwezi woyamba, umene ndi mwezi wa Nisani, chaka cha khumi ndi chiwiri cha ufumu wa Ahasiwero anachita maere, otchedwa Purimu pamaso pa Hamani kuti apeze tsiku ndi mwezi woyenera. Ndipo maere anagwera pa mwezi wa khumi ndi chiwiri ndiwo mwezi wa Adara. Kenaka Hamani anakawuza mfumu Ahasiwero kuti, “Pali mtundu wina wa anthu umene unabalalika ndipo wamwazikana pa mitundu ina mʼzigawo zonse za ufumu wanu umene miyambo yawo ndi yosiyana ndi ya anthu ena onse ndiponso amene safuna kumvera malamulo a mfumu, kotero si chinthu cha phindu kuti mfumu iwalekerere anthu otere. Ngati chingakukomereni mfumu, ikani lamulo kuti tiwawononge, ndipo ndidzalipira matalente 10,000 asiliva mosungiramo chuma cha mfumu za anthu amene adzachite ntchito imeneyi.” Choncho mfumu inavula mphete yodindira ku chala chake ndi kumupatsa Hamani mwana wa Hamedata Mwagagi, mdani wa Ayuda. Mfumu inati kwa Hamani, “Sunga ndalamazo, ndipo uchite ndi anthuwo monga ufunira.” Alembi analemba zonse zimene Hamani analamula mʼmakalata opita kwa akazembe a mfumu, abwanamkubwa a zigawo zonse ndi kwa oyangʼanira mtundu uliwonse wa anthu. Kalatazo zinali za mʼchiyankhulo cha mtundu uliwonse ndipo zinalembedwa mʼdzina la Mfumu Ahasiwero ndi kusindikizidwa ndi mphete yake. Makalatawa anawatumiza amithenga ku zigawo zonse za mfumu kuti awononge, aphe ndi kufafaniziratu a Yuda onse, anyamata, anthu okalamba, ana ndi amayi, pa tsiku limodzi la 13 la mwezi wa Adara ndipo alande katundu wawo. Mwachidule kalatayi inanena kuti mawu olembedwamowo anayenera kuperekedwa ngati lamulo mʼchigawo chilichonse ndi kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe ndi kukhala okonzeka pa tsikulo. Potsata lamulo la mfumu, amithenga aja anapita mwachangu ndipo lamuloli linaperekedwanso ku Susa, likulu la dziko. Mfumu ndi Hamani anakhala pansi ndikumamwa, koma mzinda onse wa Susa unasokonezeka. Mordekai a Pempha Estere kuti Athandize Mordekai atamva zonse zimene zinachitika, anangʼamba zovala zake, navala chiguduli ndi kudzola phulusa, ndipo analowa mu mzinda, akulira mokweza ndi mowawidwa mtima. Ndipo anapita ndi kuyima pa chipata cha mfumu, chifukwa panalibe wina aliyense amaloledwa kulowa pa chipata cha mfumu atavala chiguduli. Chigawo chilichonse kumene mawu a mfumu ndi lamulo lake zinafika, kunali maliro akulu pakati pa Ayuda. Iwo ankasala zakudya, kulira mofuwula ndi kumadandaula. Ambiri anavala ziguduli ndi kudzola phulusa. Anamwali otumikira mfumukazi Estere ndi adindo ake ofulidwa atabwera ndi kumuwuza za Mordekai, anavutika kwambiri. Estere anamutumizira zovala kuti avale ndi kuti avule chiguduli chake koma Mordekai sanalole zimenezo. Kenaka Estere anayitana Hataki, mmodzi wa adindo a mfumu ofulidwa amene anayikidwa kuti azimutumikira kuti apite kwa Mordekai kuti akamve chimene chimamuvuta komanso chifukwa chochitira zimenezi. Choncho Hataki anapita kwa Mordekai ku bwalo la mzinda patsogolo pa chipata cha mfumu. Mordekai anamuwuza zonse zimene zinamuchitikira kuphatikizapo mtengo weniweni wa ndalama zimene Hamani analonjeza kupereka mosungira chuma cha mfumu za anthu amene adzawononge a Yuda. Mordekai anamupatsanso imodzi mwa makalata a ulamuliro wonena za chiwembuchi amene anawasindikiza ku Susa kukamuonetsa ndi kumufotokozera zonse Estere. Anamuwuzanso kuti akamudandaulire kuti akapite kwa mfumu kukapempha chifundo ndi kuyidandaulira chifukwa cha anthu a mtundu wake. Hataki anabwerera ndi kumufotokozera Estere zimene Mordekai ananena. Ndipo Estere anamutuma Hataki kuti akanene kwa Mordekai kuti, “Atumiki onse amfumu ndi anthu a zigawo za mfumu ankadziwa kuti mwamuna kapena mkazi aliyense akalowa ku bwalo lake la mʼkati mosayitanidwa ndi mfumu pali lamulo limodzi: lamuloli ndi lakuti aphedwe. Zimasintha pokhapokha ngati mfumu iloza munthuyo ndi ndodo yagolide kuti akhale ndi moyo. Koma papita masiku makumi atatu ndisanayitanidwe ndi mfumu.” Tsono Mordekai anawuzidwa mawu a Estere. Kenaka Mordekai anawawuza kuti akamuyankhe Estere motere: “Usaganize kuti iwe wekha mwa Ayuda onse udzapulumuka chifukwa chakuti uli mʼnyumba ya mfumu. Pakuti ngati ukhalatu chete nthawi ino, chithandizo ndi chipulumutso cha Ayuda zidzachokera kwina nʼkutheka kuti iwe ndi a pa banja la makolo ako mudzafa. Ndipo adziwa ndani mwina unalowa ufumu chifukwa cha nthawi ngati imeneyi?” Pamenepo Estere anatumiza yankho ili kwa Mordekai: “Pitani, mukasonkhanitse pamodzi Ayuda onse amene ali mu Susa ndipo mundisalire chakudya. Musadye kapena kumwa kwa masiku atatu, usiku ndi usana. Ine ndi anamwali anga onditumikira tidzasala chakudya monga inu. Izi zikachitika, ine ndidzapita kwa mfumu, ngakhale kutero ndikutsutsana ndi lamulo. Ndipo ngati nʼkufa ndife ndithu.” Choncho Mordekai anapita ndi kuchita monga Estere anamupemphera. Pempho la Estere kwa Mfumu Tsiku lachitatu Estere anavala zovala zake zaufumu ndipo anayima mʼbwalo la mʼkati la nyumba yaufumu choyangʼana ku chipinda chachikulu cha mfumu. Mfumu inakhala pa mpando waufumu mʼchipinda chachikulu moyangʼana ku chipata cholowera mʼnyumba yaufumu. Mfumu itaona Estere atayima mʼbwalomo inakondwera naye ndipo anamuloza ndi ndodo yagolide imene inali mʼdzanja lake. Choncho Estere anayandikira ndi kukhudza msonga ya ndodoyo. Kenaka mfumu inati kwa iye, “Kodi mukufuna chiyani, inu mfumukazi Estere? Nanga pempho lanu ndi chiyani? Ngakhale mutapempha theka la ufumu, ndidzakupatsani.” Ndipo Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni, mfumu, mubwere lero pamodzi ndi Hamani kuphwando limene ndakonzera inu mfumu.” Mfumu inati, “Muwuzeni abwere Hamani msanga, kotero kuti tichite monga Estere wapempha.” Choncho mfumu ndi Hamani anafika kuphwando limene Estere anakonza. Akumwa vinyo, mfumu inamufunsano Estere kuti, “Kodi ukupempha chiyani tsopano? Chimene uti upemphe ndikupatsa. Chopempha chako ndi chiti? Ngakhale utafuna mpaka theka la ufumu, ndidzakupatsa.” Estere anayankha kuti, “Pempho langa ndi chofuna changa ndi ichi: Ngati mwandikomera mtima mfumu ndiponso ngati chingakukondweretseni mfumu kundipatsa chimene ndapempha ndi kuchita zimene ndifuna, mubwere mawa inu mfumu ndi Hamani ku phwando limene ndidzakukonzerani. Ndipo ndidzakuyankhani mfumu funso lanu.” Mkwiyo wa Hamani Ukulabe pa Mordekai Tsiku limenelo Hamani anatuluka wokondwa ndi wosangalala kwambiri. Koma ataona Mordekai pa chipata cha mfumu ndi kuti sanayimirire kapena kumupatsa ulemu pamene iye amadutsa, Hamani anamukwiyira kwambiri, komabe Hamani anadziletsa ndipo anapita ku nyumba kwake. Anayitana abwenzi ake pamodzi ndi mkazi wake Zeresi. Hamani anawawuza za kuchuluka kwa chuma chake ndi kuti anali ndi ana aamuna ambiri. Anawawuzanso za mmene mfumu inamukwezera ndi kumuyika kukhala woposa nduna ndi olemekezeka onse. Hamani anawonjeza kuti, “Ndipotu si zokhazi. Ndine ndekha amene ndayitanidwa pamodzi ndi mfumu kuphwando limene mfumukazi Estere anatikonzera. Ndipo mawa wandiyitananso pamodzi ndi mfumu. Koma zonsezi sindikhutira nazo ndikamaona nthawi zonse Myuda uja Mordekai atakhala pa chipata cha mfumu.” Mkazi wake Zeresi ndi abwenzi ake onse aja anamuwuza kuti, “Anthu apange mtanda wotalika mamita 23 ndipo mmawa upemphe mfumu kuti anthu akhomerepo Mordekai. Kenaka upite ndi mfumu kuphwando mokondwa.” Hamani anakondwera ndi uphungu umenewu ndipo mtanda unapangidwa. Mordekai Apatsidwa Ulemu Usiku umenewo mfumu inalephera kugona tulo; Choncho inayitanitsa buku limene amalembamo mbiri ya zamakedzana kuti amuwerengere. Anapeza kuti mʼbukumo munalembedwa zoti Mordekai anawulula kuti Bigitana ndi Teresi, awiri mwa adindo ofulidwa a mfumu amene ankalondera pa khomo la chipinda cha mfumu ndiwo anakonza chiwembu chofuna kupha mfumu Ahasiwero. Mfumu inafunsa kuti, “Kodi Mordekai anamupatsa ulemu ndi ukulu wotani chifukwa cha chinthu chimene anachitachi?” Atumiki ake anamuyankha kuti, “Palibe chimene chinachitika kwa iye.” Mfumu inati, “Kodi ndani ali mʼbwalomo?” Tsono Hamani anali atangolowa kumene mʼbwalo lakunja la nyumba yaufumu kuti akawuze mfumu zomukhomera Mordekai pa mtanda umene anamukonzera. Atumiki ake anamuyankha kuti, “Hamani ndiye wayima mu bwalo.” “Mulowetseni,” Mfumu inalamulira. Hamani atalowa, mfumu inamufunsa kuti, “Kodi timuchitire ulemu otani munthu amene mfumu ikondweretsedwa naye?” Tsono Hamani anaganiza mu mtima kuti, “Kodi palinso ndani amene mfumu ingamulemekeze kuposa ine?” Choncho Hamani anayankha mfumuyo kuti, “Munthu amene mfumu ifuna kumuchitira ulemu, imuchitire izi: Anthu abwere ndi chovala cha ufumu ndi kavalo amene mfumu imakwerapo wokhala ndi chizindikiro chaufumu pamutu pake. Ndipo mupereke chovala cha ufumucho ndi kavalo kwa mmodzi wa akalonga a mfumu a ulemu kwambiri. Ameneyu amuveke chovalacho munthu amene mfumu yakondweretsedwa naye. Akavekedwa chovalachi amuyendetse mʼmisewu yonse ya mzinda atakwera pa kavalo wa mfumu. Kalongayu azifuwula patsogolo pa munthuyu kuti ‘Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!’ ” Mfumu inalamulira Hamani kuti, “Pita msanga, katenge chovala cha ufumu ndi kavalo ndipo uchite monga wanenera kwa Mordekai Myuda, amene amakhala pa chipata cha mfumu. Usasiyeko china chilichonse chimene wanena.” Choncho Hamani anatenga chovala ndi kavalo. Anamuveka Mordekai chovalacho ndipo anamuyendetsa mʼmisewu yonse ya mu mzinda atakwera pa kavalo, akufuwula kuti, “Ichi ndi chimene mfumu yachita kwa munthu amene yafuna kumuchitira ulemu!” Pambuyo pake Mordekai anabwerera ku chipata cha mfumu. Koma Hamani anapita msanga ku nyumba kwake, akulira, atafundira mutu wake. Hamani anawuza Zeresi mkazi wake ndi abwenzi ake onse zonse zinamuchitikira. Anthu ake anzeru ndi mkazi wake Zeresi anamuwuza kuti, “Popeza kuti Mordekai ndi Myuda amene mwayamba kale kugonja pamaso pake, ndiye kuti palibe chimene mungachitepo. Mudzagwa ndithu pamaso pake.” Pamene anthuwa amayankhula nayebe, adindo a mfumu ofulidwa anabwera kudzamutenga Hamani mofulumira kupita naye ku phwando limene Estere anakonza. Hamani Aphedwa Choncho mfumu ndi Hamani anabwera kudzadya phwando la mfumukazi Estere. Pa tsiku lachiwiri akumwa vinyo, mfumu inafunsanso kuti, “Kodi iwe mfumukazi Estere, chimene ufuna kupempha nʼchiyani? Chimene uti upemphe ndidzakupatsa. Choncho ukufuna chiyani? Ngakhale utafuna theka la ufumu ndidzakupatsa.” Kenaka mfumukazi Estere anayankha kuti, “Ngati mwandikomera mtima, inu mfumu, ndipo ngati chingakukomereni mfumu, pempho ndi chokhumba changa ndi ichi, mulole kuti ine ndi abale anga tisungidwe tonse ndi moyo. Popeza ine ndi anthu a mtundu wanga tagulitsidwa kuti atiwononge, atiphe ndi kutifafaniziratu. Akanangotigulitsa kokha tikanakhala chete, chifukwa chimene mdani wathuyo akanakupatsani mfumu sibwenzi mutasowa nacho mtendere.” Mfumu Ahasiwero anamufunsa mfumukazi Estere, “Kodi iyeyu ndi ndani ndipo ali kuti amene saopa kuchita chinthu chotere?” Estere anati, “Wotizunza ndiponso mdani wathu! Munthu woyipayo ndi Hamani.” Kenaka Hamani anagwidwa ndi mantha pamaso pa mfumu ndi mfumukazi. Mfumu itakwiya kwambiri inanyamuka pa phwando nipita ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu. Koma Hamani, pozindikira kuti mfumu yaganiza kale kumuchitira choyipa, anatsalira mʼnyumba kupempha Estere kuti apulumutse moyo wake. Mfumu itabwerera kuchokera ku munda wa maluwa wa nyumba yaufumu uja ndi kulowanso mʼchipinda chaphwando, anapeza Hamani atagona chafufumimba pa mpando wa khutagone pomwe Estere anakhalapo. Mfumu inayankhula mokweza kuti, “Kodi afunanso kuvula mfumukazi momukakamiza pamene ine ndili mʼnyumba?” Mfumu isanatsirize kuyankhula mawu awa, atumiki ake anaphimba nkhope ya Hamani. Haribona, mmodzi wa adindo ofulidwa amene ankatumikira mfumu anati, “Mtanda wotalika mamita 23 uli mʼnyumba ya Hamani. Mtandawu, Hamani anapangira Mordekai, uja amene anapulumutsa mfumu ku chiwembu.” Mfumu inati, “Mpachikeni pamenepo!” Choncho anamupachika Hamani pa mtanda umene anakonzera Mordekai. Kenaka mkwiyo wa mfumu unatsika. Lamulo la Mfumu Lothandiza Ayuda Tsiku lomwelo mfumu Ahasiwero anamupatsa mfumukazi Estere nyumba ya Hamani, mdani wa Ayuda. Ndipo Mordekai anafika pamaso pa mfumu, popeza Estere anamuwuza ubale wawo. Mfumu inavula mphete yake yodindira imene analanda kwa Hamani ndipo Estere anamusankha Mordekai kukhala woyangʼanira nyumba ya Hamani. Estere anayankhulanso ndi mfumu ndipo anadzigwetsa pa mapazi ake. Uku akulira iye anapempha mfumu kuti iletse choyipa, makamaka chiwembu chimene Hamani Mwagagi anakonza kuti awononge a Yuda. Ndipo mfumu inamuloza Estere ndi ndodo yake yagolide ndipo Estere anadzuka ndi kuyima pamaso pake. Iye anati, “Ngati chikomera mfumu ndi kukukondweretsani, ngati pempho langa muliona kuti ndi loyenera ndi kuti mukondwera nane tsono mfumu ilole kuti lamulo lilembedwe kusintha mawu a mʼmakalata amene Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, anatumiza ku zigawo zonse za mfumu. Paja Hamani analemba kuti Ayuda onse awonongedwe. Kodi ndingapirire bwanji pamene ndi kuona tsoka likugwera anthu a mtundu wanga? Ndingapirire bwanji pamene abale anga akuwonongedwa?” Mfumu Ahasiwero anamuyankha mfumukazi Estere ndi Mordekai Myuda kuti, “Ndapereka nyumba ya Hamani kwa Estere ndipo Hamaniyo amupachika kale pa mtanda chifukwa anafuna kuwononga Ayuda. Tsono inu awiri, lembani za Ayudawo monga mufunira. Mulembe mʼdzina la mfumu ndipo musindikize chizindikiro cha mphete ya mfumu popeza kuti cholembedwa mʼdzina la mfumu ndi kusindikizidwa ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu sichingasinthidwe.” Nthawi yomweyo, pa tsiku la 23 la mwezi wachitatu wa Sivani, mfumu inayitana alembi ake. Analemba zonse zokhudza Ayuda monga ananenera Mordekai. Analembera akazembe, abwanamkubwa ndi nduna za zigawo 127 kuyambira ku India mpaka ku Kusi. Zimene analamula Mordekai zinalembedwa mʼzilembo za chigawo chilichonse ndi chiyankhulo cha mtundu uliwonse wa anthu. Ayudanso anawalembera mʼmalemba awo ndi chiyankhulo chawo. Mordekai analemba makalatawo mʼdzina la mfumu Ahasiwero, nawadinda ndi chizindikiro cha mphete ya mfumu. Ndipo anawatumiza ndi anthu amithenga amene anakwera pa akavalo a ufumu othamanga kwambiri obadwa mu khola la ufumu. Mʼmakalata amenewa mfumu inalola kuti Ayuda okhala mu mzinda uliwonse akhale ndi ufulu wokumana ndi kudzitchinjiriza komanso kuwononga, kupha ndi kufafaniziratu gulu lililonse la nkhondo la anthu a mtundu uliwonse kapena chigawo chimene chingawathire nkhondo. Ayudawo analoledwa kuwononga gulu lankhondo lija, ana awo ndi akazi awo komanso kuti afunkhe katundu wawo. Ayuda analoledwa kuchita zimenezi mʼzigawo zonse za Mfumu Ahasiwero pa tsiku limodzi lokha la 13 la mwezi wa 12, mwezi wa Adara. Mawu a mʼmakalatawo anayenera kudziwitsidwa kwa anthu a mtundu uliwonse mu chigawo chilichonse kuti ndi lamulo ndithu kwa anthu a mtundu uliwonse ndi kuti Ayuda adzakhale okonzeka pa tsikulo kulipsira kwa adani awo. Atawalamulira a mfumu, amithenga aja anapita nawo makalata mwachangu, atakwera pa akavalo a mfumu. Ndipo lamulolo analiperekanso ku likulu la mzinda wa Susa. Mordekai anachoka pamaso pa mfumu atavala zovala zaufumu zooneka ngati mtambo ndi zofewa zoyera, chipewa chachikulu cha golide ndi mkanjo wapepo. Ndipo mzinda wa Susa unafuwula mokondwa. Kwa Ayuda inali nthawi ya nkhope zowala ndi za chimwemwe, chikondwerero ndi ulemu. Mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse, kumene mawu a mfumu onena za lamulo lake anafika, kunali chimwemwe ndi chikondwerero pakati pa Ayuda. Linali tsiku la phwando ndi chikondwerero. Ndipo anthu ambiri a mitundu ina anazitcha Ayuda chifukwa anachita mantha ndi Ayudawo. Chigonjetso cha Ayuda Pa mwezi wa 12, mwezi wa Adara pa tsiku la 13 la mwezi womwewo, tsiku limene lamulo loyamba lija la mfumu linayembekezereka kuti litsatidwe, pamene adani a Ayuda anati awononge Ayudawo, zinthu zinasintha. Ayuda ndiwo anawononga adani awo. Ayuda anasonkhana mʼmizinda ya zigawo zonse za Mfumu Ahasiwero kuthira nkhondo onse amene anafuna kuwawononga. Palibe amene akanalimbana nawo chifukwa anthu onse a mitundu ina anachita nawo mantha. Ndipo akuluakulu onse a zigawo, akalonga, akazembe ndi ogwira ntchito za mfumu anathandiza Ayuda, chifukwa anachita mantha ndi Mordekai. Pajatu Mordekai anali munthu wamkulu mʼnyumba ya ufumu. Mbiri yake inafalikira zigawo zonse, ndipo mphamvu zake zinakulirakulirabe. Motero Ayuda anakantha adani awo onse ndi lupanga, kuwapha ndi kuwawononga, ndipo anachita chimene chinawakomera kwa adani awo. Ku likulu la mzinda wa Susa, Ayuda anapha ndi kuwononga anthu 500. Ayuda anaphanso Parisandata, Dalifoni, Asipata, Porata, Adaliya, Aridata, Parimasita, Arisai, Aridai ndi Vaisata, ana khumi a Hamani, mwana wa Hamedata, mdani wa Ayuda. Koma sanalande katundu wawo. Tsiku lomwelo anawuza mfumu chiwerengero cha anthu amene anaphedwa mu likulu la mzinda wa Susa. Mfumu inati kwa mfumukazi Estere, “Ayuda apha ndi kuwononga anthu 500 ndi ana khumi a Hamani mu likulu la mzinda wa Susa. Nanga ku zigawo zina zonse za mfumu achitako chiyani? Kodi tsopano ukupemphanso chiyani? Chimene ukupempha ndidzakupatsa. Kodi ukufuna chiyani? Chimene ukufuna ndidzakupatsa.” Estere anayankha kuti, “Ngati chingakukomereni mfumu, apatseni chilolezo Ayuda okhala mu Susa kuti achitenso zimene achita lerozi mawa, potsata lamulo ndipo mulole kuti ana khumi a Hamani aja mitembo yawo ipachikidwe pa mtanda.” Choncho mfumu inalamula kuti izi zichitike. Anapereka lamulo mu Susa ndipo mitembo ya ana khumi a Hamani anayipachika pa mtanda. Ayuda a mu mzinda wa Susa anasonkhana pamodzi pa tsiku la 14 la mwezi wa Adara ndipo anapha anthu 300 mu Susa, koma sanatenge katundu wawo. Tsono Ayuda ena onse amene anali mu zigawo za mfumu anasonkhananso kudziteteza ndipo sanasautsidwenso ndi adani popeza anapha anthu 75,000 koma sanalande zofunkha zawo. Zonsezi zinachitika pa tsiku la 13 la mwezi wa Adara ndipo pa tsiku la 14 anapumula ndi kupanga tsikuli kuti likhale la madyerero ndi chikondwerero. Kukondwerera Purimu Koma Ayuda okhala mu Susa anasonkhana pa tsiku la 13 ndi la 14 ndipo anakonza tsiku la 15 kuti likhale tsiku la madyerero ndi chikondwerero. Ichi ndi chifukwa chake Ayuda a ku midzi, amene amakhala mʼzithando amasunga tsiku la 14 la mwezi wa Adara ngati la madyerero ndi chikondwerero, tsiku lopatsana mphatso. Mordekai analemba mawu awa mʼmakalata ndipo anawatumiza kwa Ayuda onse okhala mʼzigawo zonse za mfumu Ahasiwero, a pafupi ndi a kutali: Anati chaka chilichonse, Ayudawo azisunga tsiku la 14 ndi 15 la mwezi wa Adara, ngati masiku amene Ayuda anapulumutsidwa kwa adani awo, ndiponso ngati mwezi umene chisoni chawo chinasandulika chimwemwe ndi kulira kwawo kunasandulika chikondwerero. Anawalembera kuti azisunga masikuwa ngati masiku a madyerero ndi chikondwerero, masiku opatsana mphatso zachakudya kwa wina ndi mnzake komanso opereka mphatso kwa osauka. Choncho Ayuda anavomereza kusunga masikuwa ngati a chikondwerero monga analembera Mordekai. Hamani mwana wa Hamedata, Mwagagi, mdani wa Ayuda onse, anakonza chiwembu chakupha ndi kuwononga Ayuda ndipo anachita maere otchedwa Purimu kuti awaphe ndi kuwawononga. Koma mfumu itazindikira za chiwembuchi, inalamula kuti zilembedwe mʼmakalata kuti chiwembu chimene Hamani anakonzera Ayuda chigwere pa iye mwini, ndi kuti iye pamodzi ndi ana ake apachikidwe pa mtanda. Ndi chifukwa chake masiku amenewa amatchedwa masiku a Purimu potsata dzina lakuti Purimu. Chifukwa cha kalata ya Mordekai ndiponso chifukwa cha zimene anaziona ndi kuwachitikira, Ayuda onse anagwirizana kukhazikitsa lamulo lokhudza iwo, zidzukulu zawo ndi onse amene adzapanga nawo ubale kuti asalephere kusunga masiku awiri amenewa chaka chilichonse monga zinalembedweramo ndiponso potsata nthawi imene anayika. Azisunga ndi kukumbukira masiku amenewa mu mʼbado uliwonse ndi banja lililonse, mʼchigawo chilichonse ndi mu mzinda uliwonse. Ndipo Ayuda asadzasiye kukondwerera masiku a Purimuwa ndiponso zidzukulu zawo zisadzaleke kuwakumbukira. Choncho mfumukazi Estere, mwana wa mkazi wa Abihaili, pamodzi ndi Mordekai Myuda analemba ndi ulamuliro onse kutsimikizira kalata iyi yachiwiri yokhudza Purimu. Ndipo Mordekai anatumiza makalata kwa Ayuda onse ku zigawo 127 za ufumu wa Ahasiwero. Kalatayi inali ya mawu a mtendere ndiponso a kukhulupirika kuti azisunga masiku a Purimu pa nyengo imene inavomerezeka monga mmene Mordekai Myuda ndi mfumukazi Estere anawalamulira ndiponso monga anadziyikira eni okha ndi zidzukulu zawo zonena za nthawi zawo za kusala zakudya ndi kulira. Lamulo la Estere linakhazikitsa mwambo wa Purimuwu ndipo zinalembedwa mʼmabuku. Ukulu wa Mordekai Mfumu Ahasiwero anakhometsa msonkho mʼdziko lake lonse mpaka ku zilumba zonse. Ndipo ntchito zonse zochitika ndi mphamvu zake komanso ndi zonse zofotokoza za ukulu wa Mordekai, kukwezedwa kwake ndi mfumu, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Mediya ndi Peresiya? Pakuti Mordekai Myuda uja anali wachiwiri wa mfumu Ahasiwero. Kwa Ayuda onse Mordekai anali munthu wamkulu ndipo ankamukonda chifukwa ankachitira zabwino mtundu wake ndi kufunira mtendere abale ake.