- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 AEFESO Kalata ya Paulo Yolembera Aefeso Aefeso Aef KALATA YA PAULO YOLEMBERA AEFESO Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu. Kulembera oyera mtima a ku Efeso, okhulupirika mwa Khristu Yesu: Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu. Madalitso Auzimu mwa Khristu Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, amene anatipatsa madalitso onse a uzimu kumwamba mwa Khristu. Dziko lapansi lisanalengedwe, Mulungu anatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi wopanda cholakwa pamaso pake. Mwa chikondi chake, Iye anakonzeratu kuti ife titengedwe ngati ana mwa Yesu Khristu, molingana ndi kukonda kwake ndi chifuniro chake. Anachita zimenezi kuti tiziyamika ulemerero wa chisomo chake, umene watipatsa kwaulere mwa Khristu amene amamukonda. Mwa Yesu Khristu, chifukwa cha magazi ake, ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo athu molingana ndi kuchuluka kwa chisomo cha Mulungu chimene anatipatsa mosawumira. Mwa nzeru zonse ndi chidziwitso, Iye watiwululira chifuniro chake chimene chinali chobisika, chimene anachikonzeratu mwa Khristu, molingana ndi kukoma mtima kwake. Chimene anakonza kuti chichitike nʼchakuti, ikakwana nthawi yake asonkhanitsa pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za kumwamba ndi pa dziko lapansi. Iye anatisankhiratu mwa Khristu, atatikonzeratu molingana ndi machitidwe a Iye amene amachititsa zinthu zonse kuti zikwaniritse cholinga cha chifuniro chake, nʼcholinga chakuti, ife amene tinali oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu, tiyamike ulemerero wake. Ndipo inunso pamene munamva mawu a choonadi, Uthenga Wabwino wa chipulumutso chanu, munayikidwanso mwa Khristu. Mutakhulupirira, anakusindikizani chizindikiro pokupatsani Mzimu Woyera amene Iye analonjeza. Mzimu Woyerayo ndi chikole chotsimikizira kuti tidzalandira madalitso athu, ndipo kuti Mulungu anatiwombola kuti tikhale anthu ake. Iye anachita zimenezi kuti timuyamike ndi kumulemekeza. Kuyamika ndi Kupemphera Choncho, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chanu mwa Ambuye Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse, ine sindilekeza kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani mʼmapemphero anga. Ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate a ulemerero akupatseni mzimu wa nzeru ndi wa vumbulutso, kuti mumudziwe kwenikweni. Ndimapempheranso kuti maso a mitima yanu atsekuke ndi cholinga choti mudziwe chiyembekezo chimene Iye anakuyitanirani, chuma cha ulemerero chomwe chili mwa anthu oyera mtima. Ndiponso ndikufuna kuti mudziwe mphamvu zake zazikulu koposa zimene zili mwa ife amene timakhulupirira. Mphamvuyi ndi yofanana ndi mphamvu yoposa ija imene inagwira ntchito pamene Mulungu anaukitsa Khristu kwa akufa, namukhazika Iye ku dzanja lake lamanja mʼdziko la kumwamba. Anamukhazika pamwamba pa ulamuliro onse ndi mafumu, mphamvu ndi ufumu, ndiponso pamwamba pa dzina lililonse limene angalitchule, osati nthawi ino yokha komanso imene ikubwerayo. Ndipo Mulungu anayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake ndi kumusankha Iyeyo kukhala mutu pa chilichonse chifukwa cha mpingo, umene ndi thupi lake, chidzalo cha Iye amene adzaza chilichonse mu njira iliyonse. Amene anali Akufa Alandira Moyo Kunena za inu, kale munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu, mmene inu munkakhalamo pamene munkatsatira njira za dziko lapansi ndi za ulamuliro waufumu wa mlengalenga, mzimu umene ukugwira ntchito tsopano mwa amene samvera. Nthawi ina tonsefe tinalinso ndi moyo wonga wawo, tinkachitanso zilizonse zimene matupi ndi maganizo athu ankafuna. Mwachibadwa chathu, tinali oyenera chilango monga anthu ena onse. Koma chifukwa cha chikondi chake chachikulu pa ife, Mulungu amene ndi olemera mʼchifundo, anatipanga kukhala amoyo ndi Khristu ngakhale pamene ife tinali akufa mu zolakwa zathu. Koma tinapulumutsidwa mwachisomo. Ndipo Mulungu anatiukitsa pamodzi ndi Khristu ndi kutikhazika pamodzi ndi Iye mmwamba mwa Khristu Yesu, ndi cholinga chakuti mʼnthawi imene ikubwera, Iyeyo adzaonetse chuma choposa cha chisomo chake, choonetsedwa mwa kukoma mtima kwake kwa ife mwa Khristu Yesu. Pakuti mwapulumutsidwa mwachisomo, kudzera mʼchikhulupiriro ndipo izi sizochokera mwa inu eni, koma ndi mphatso ya Mulungu, osati ndi ntchito, kuti wina aliyense asadzitamandire. Pakuti ndife ntchito ya Mulungu, olengedwa mwa Khristu Yesu kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anazikonzeratu kale kuti tizichite. Umodzi mwa Khristu Chifukwa chake kumbukirani kuti poyamba inu amene munali anthu a mitundu ina mwachibadwa ndipo munkatchedwa “osachita mdulidwe” ndi amene amadzitcha okha “a mdulidwe” (zimene zinachitika mʼthupi ndi manja a anthu). Kumbukirani kuti nthawi imene inu munali wopanda Khristu, simunkawerengedwa ngati nzika za Israeli ndipo munali alendo pa pangano la lonjezo, wopanda chiyembekezo ndi opanda Mulungu mʼdziko lapansi. Koma tsopano mwa Khristu Yesu, inu amene nthawi ina munali kutali, mwabweretsedwa pafupi kudzera mʼmagazi a Khristu. Pakuti Iye mwini ndiye mtendere wathu, amene anachita kuti awiri akhale mmodzi ndipo anagumula chotchinga, khoma la udani lotilekanitsa, pothetsa mʼthupi lake lamulo pamodzi ndi zolamulira zake ndi malangizo. Cholinga chake chinali chakuti alenge mwa Iye mwini, munthu mmodzi watsopano kuchokera kwa abwino, motero nʼkupanga mtendere, ndi kuyanjanitsa onse awiriwa mʼthupi lake kwa Mulungu, kudzera pa mtanda, umene Iye anaphapo udani wawo. Iye anabwera ndipo analalikira mtendere kwa inu amene munali kutali ndi mtendere ndiponso kwa iwonso amene anali pafupi. Pakuti mwa Iye, ife tonse titha kufika kwa Atate mwa Mzimu mmodzi. Kotero kuti, inu sindinunso alendo ndi adani, koma nzika pamodzi ndi anthu a Mulungu ndiponso a mʼbanja la Mulungu. Ndinu okhazikika pa maziko a atumwi ndi a aneneri, pamodzi ndi Khristu Yesu mwini ngati mwala wa pa ngodya. Mwa Iyeyo, nyumba yonse yalumikizidwa pamodzi ndipo yakwezedwa kukhala Nyumba yoyera mwa Ambuye. Ndipo mwa Iye, inunso mukamangidwa pamodzi ndi ena onse kukhala nyumba yokhalamo imene Mulungu amakhala mwa Mzimu wake. Paulo Mlaliki wa Anthu a Mitundu Ina Nʼchifukwa chake ine Paulo, ndili wamʼndende wa Khristu Yesu chifukwa cha inu anthu a mitundu ina. Ndithudi, inu munamva za ntchito yachisomo cha Mulungu imene anandipatsa chifukwa cha inu, ndicho chinsinsi chimene chinawululidwa kwa ine mwa vumbulutso, monga ndinakulemberani kale mwachidule. Pamene mukuwerenga izi, inu mudzazindikira za chidziwitso changa pa chinsinsi cha Khristu, chimene sichinawululidwe kwa anthu amibado ina monga momwe tsopano chawululidwa ndi Mzimu wa Mulungu mwa atumwi oyera ndi aneneri. Chinsinsicho nʼchakuti, kudzera mu Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina ndi olowamʼmalo pamodzi ndi Aisraeli, ndi ziwalo za thupi limodzi, ndi olandira nawo pamodzi malonjezo a mwa Khristu Yesu. Mwachisomo cha Mulungu ndi mphamvu zake, ine ndinasanduka mtumiki wa Uthenga Wabwinowu. Ngakhale ndili wamngʼono kwambiri pakati pa anthu onse a Mulungu, anandipatsa chisomo chimenechi cholalikira kwa anthu a mitundu ina chuma chopanda malire cha Khristu. Ndinasankhidwa kuti ndifotokoze momveka bwino kwa munthu aliyense za chinsinsi chimenechi, chinsinsi chimene kuyambira kale chinali chobisika mwa Mulungu amene analenga zinthu zonse. Cholinga chake tsopano nʼchakuti, kudzera mwa mpingo, mafumu ndi a ulamuliro onse a kumwamba adziwe nzeru zochuluka za Mulungu. Chimenechi chinali chikonzero chamuyaya cha Mulungu, chimene chinachitika kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye athu. Mwa Khristu ndi mwa chikhulupiriro chathu mwa Iye, timayandikira kwa Mulungu momasuka ndi molimbika mtima. Choncho, ine ndikukupemphani kuti musakhumudwe popeza ndikusautsidwa chifukwa cha inu pakuti masautso angawa ndi ulemerero wanu. Paulo Apempherera Aefeso Nʼchifukwa chake ine ndikugwada pamaso pa Atate, amene banja lililonse kumwamba ndi pa dziko lapansi limatchulidwa ndi dzina lawo. Ndikupemphera kuti kuchokera mʼchuma cha ulemerero wake alimbikitse moyo wanu wa mʼkati ndi mphamvu za Mzimu wake, kuti Khristu akhazikike mʼmitima mwanu mwachikhulupiriro. Ndipo ndikukupemphererani kuti muzikike ndi kukhazikika mʼchikondi kuti mukhale ndi mphamvu, kuti pamodzi ndi anthu oyera mtima onse muthe kuzindikira kupingasa, kutalika ndi kukwera komanso kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu. Ndikukupemphererani kuti mudziwe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kwathunthu ndi moyo wa Mulungu mwini. Tsopano kwa Iye amene angathe kuchita zochuluka kuposa zimene tingapemphe, kapena kuganiza molingana ndi mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwa ife, Iyeyo akhale ndi ulemu mu mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibado yonse mpaka muyaya. Ameni. Umodzi Mʼthupi la Khristu Ine monga wamʼndende chifukwa chotumikira Ambuye, ndikukulimbikitsani kuti mukhale moyo woyenera mayitanidwe amene munalandira. Mukhale odzichepetsa kwathunthu ndi ofatsa; mukhale oleza mtima, ololerana wina ndi mnzake mwachikondi. Muyesetse kusunga umodzi wa Mzimu; umodzi umene umatimangirira pamodzi mu mtendere. Pali thupi limodzi ndiponso Mzimu mmodzi, monganso pali chiyembekezo chimodzi chimene anakuyitanirani. Pali Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi; Mulungu mmodzi ndi Atate a onse, ndipo ali mwa onse. Koma aliyense wa ife wapatsidwa chisomo molingana ndi muyeso wa mphatso ya Khristu. Nʼchifukwa chake akunena kuti, “Iye atakwera kumwamba, anatenga chigulu cha a mʼndende ndipo anapereka mphatso kwa anthu.” Kodi mawu akuti, “Iye anakwera” akutanthauza chiyani, ngati Iyeyo sanatsikire kunsi kwa dziko lapansi? Iye amene anatsika ndi yemweyo anakwera koposa mʼmayiko a kumwamba onse, ndi cholinga choti zinthu zonse zikhale zodzaza ndi Iye. Iye ndiye amene anapereka mphatso kwa ena kuti akhale atumwi ndi ena aneneri, ena alaliki, ndi ena abusa ndi aphunzitsi. Ntchito yawo ndi kukonza oyera mtima kuti agwire ntchito ya utumiki kuti thupi la Khristu lilimbikitsidwe. Izi zidzatifikitsa tonse ku umodzi wachikhulupiriro, kumudziwa Mwana wa Mulungu, kukhwima msinkhu ndi kufika pa muyeso wangwiro weniweni wopezeka mwa Khristu. Motero sitidzakhalanso makanda, ogwedezekagwedezeka ndi mafunde, otengekatengeka ndi mphepo iliyonse ya chiphunzitso ndi kuchenjera kwa anthu achinyengo amene amasocheretsa anthu ndi kuchenjera kwawo. Mʼmalo mwake, poyankhula choonadi mwachikondi, tidzakula mu zinthu zonse ndi kukhala thupi la Khristu, amene ndi Mutu, omwe ndi mpingo. Mwa Iye thupi lonse lalumikizidwa ndi kugwirana pamodzi ndi mitsempha yothandizira. Likukula ndi kudzilimbitsa lokha mwachikondi, pomwe chiwalo chilichonse chikugwira ntchito yake. Malangizo pa Makhalidwe a Chikhristu Tsono ine ndikukuwuzani izi, ndipo ndikunenetsa mwa Ambuye, kuti musayendenso monga amachitira anthu a mitundu ina potsata maganizo awo opanda pake. Maganizo awo ndi odetsedwa, ndi osiyanitsidwa ndi moyo wa Mulungu chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo chifukwa cha kuwuma mtima kwawo. Popeza sazindikiranso kanthu kalikonse, adzipereka okha kuti akhumbe zonyansa, kuti achite mtundu uliwonse wa zoyipa ndi zilakolako zosatha. Koma inu simunadziwe Khristu mʼnjira yotere. Zoonadi munamva za Iye ndipo munaphunzitsidwa mwa Iye molingana ndi choonadi chimene chili mwa Yesu. Inu munaphunzitsidwa molingana ndi moyo wanu wakale, kuchotsa umunthu wakale, umene ukupitirira kuwonongeka ndi zilakolako zachinyengo; kuti mukonzedwe mwatsopano mʼmitima mwanu; ndi kuti muvale umunthu watsopano, wolengedwa kuti ufanane ndi Mulungu mu chilungamo chenicheni ndi chiyero. Chifukwa chake, aliyense wa inu aleke kunama ndipo ayankhule zoona kwa mʼbale wake, pakuti ife tonse ndife ziwalo za thupi limodzi. Kwiyani koma musachimwe. Dzuwa lisalowe mukanali chikwiyire. Musamupatse mpata Satana. Iye amene wakhala akuba asabenso, koma agwire ntchito ndi kuchita kenakake kaphindu ndi manja ake, kuti akhale ndi kenakake kogawana ndi amene akusowa. Mʼkamwa mwanu musatuluke mawu aliwonse onyansa, koma okhawo amene ndi othandiza kulimbikitsa ena molingana ndi zosowa zawo, kuti athandize amene akawamve. Ndipo musamvetse chisoni Mzimu Woyera wa Mulungu amene mwasindikizidwa naye chizindikiro cha tsiku la kuwomboledwa. Chotsani kuzondana, ukali ndi kupsa mtima, chiwawa ndi kuyankhula zachipongwe, pamodzi ndi choyipa chilichonse. Mukomerane mtima ndi kuchitirana chifundo wina ndi mnzake. Khululukiranani wina ndi mnzake, monga momwe Mulungu anakukhululukirani mwa Khristu. Choncho, monga ana okondedwa, tsatirani chitsanzo cha Mulungu. Muzikondana monga Khristu anakonda ife nadzipereka yekha chifukwa cha ife monga chopereka cha fungo lokoma ndi nsembe kwa Mulungu. Koma pakati panu pasamveke nʼpangʼono pomwe zadama, kapena za mtundu wina uliwonse wa chodetsa, kapena za umbombo, chifukwa izi ndi zosayenera kwa anthu oyera a Mulungu. Musamatukwane, kuyankhula zopusa kapena kunena nthabwala zopanda pake, zomwe ndi zosayenera, koma mʼmalo mwake muziyamika. Dziwani ichi, palibe wadama, wochita zonyansa kapena waumbombo, munthu wotero ali ngati wopembedza mafano, amenewa alibe malo mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu. Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere. Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. Nʼchifukwa chake Malemba akuti, “Dzuka, wamtulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuwalira.” Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu. Malangizo kwa Akazi ndi Amuna Mʼbanja Gonjeranani wina ndi mnzake, kuonetsa kuopa Khristu. Inu akazi, muzigonjera amuna anu, monga mumagonjera kwa Ambuye. Pakuti mwamuna ndi mutu wa mkazi monga momwe Khristu ali mutu wa mpingo, thupi lake, limene Iyeyo ndi Mpulumutsi wake. Tsono monga mpingo umagonjera Khristu, momwemonso akazi akuyenera kugonjera amuna awo mu zonse. Inu amuna, kondani akazi anu monga momwe Khristu anakondera mpingo nadzipereka yekha mʼmalo mwa mpingowo kuti awupatule ukhale oyera, atawuyeretsa powusambitsa ndi madzi omwe ndi mawu ake. Anachita zimenezi kuti awupereke mpingowo kwa Iye mwini, mpingo wowala ndi waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapena chilema chilichonse, koma oyera ndi wangwiro. Momwemonso, amuna akuyenera kukonda akazi awo monga matupi awo. Iye amene akonda mkazi wake adzikondanso yekha. Pakuti palibe amene amadana nalo thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamalira bwino, monga momwe Khristu amachitira ndi mpingo wake pakuti ndife ziwalo za thupi lake. “Pa chifukwa ichi, mwamuna adzasiya abambo ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.” Ichi ndi chinsinsi chozama, koma ine ndikunena za Khristu ndi mpingo. Chomwecho, aliyense mwa inu akuyenera kukonda mkazi wake monga adzikondera iye mwini, ndipo mkazi akuyenera kulemekeza mwamuna wake. Ana ndi Makolo Awo Inu ana, mverani makolo anu mwa Ambuye, pakuti zimenezi ndi zoyenera. “Lemekeza abambo ndi amayi ako.” Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Ngati ulemekeza abambo ako ndi amayi ako, “zinthu zidzakuyendera bwino ndipo udzasangalala ndi moyo wautali pa dziko lapansi.” Abambo musakwiyitse ana anu; mʼmalo mwake, muwalere mʼchiphunzitso ndi mʼchilangizo cha Ambuye. Antchito ndi Mabwana Awo Inu antchito, mverani mabwana anu mwaulemu ndi mwamantha ndi moona mtima, monga momwe mungamvere Khristu. Musawamvere pamene akukuonani kuti akukomereni mtima, koma ngati akapolo a Khristu ochita chifuniro cha Mulungu kuchokera mu mtima mwanu. Tumikirani ndi mtima wonse, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu. Inu mukudziwa kuti Ambuye adzamupatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene anagwira, kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu. Ndipo inu mabwana, muziwachitiranso chimodzimodzi antchito anu. Musamawaopseze, popeza mukudziwa kuti Mbuye wawo ndi wanunso, nonse Mbuye wanu ali kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho. Zida Zankhondo za Mulungu Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse. Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera. Mawu Otsiriza Tukiko, mʼbale wanga wokondedwa ndi mtumiki wokhulupirika mwa Ambuye, adzakuwuzani zonse kuti inunso mudziwe mmene ndilili ndi zimene ndikuchita. Ine ndikumutumiza kwa inu, kuti mudziwe za moyo wathu, ndi kuti akulimbikitseni. Mtendere, chikondi pamodzi ndi chikhulupiriro kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi abale onse. Chisomo kwa onse amene amakonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosatha.