- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
AKOLOSE
Kalata ya Paulo Yolembera Akolose
Akolose
Akol
KALATA YA PAULO YOLEMBERA
AKOLOSE
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, ndi Timoteyo mʼbale wathu.
Kulembera abale oyera mtima ndi okhulupirira a ku Kolose mwa Khristu.
Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu.
Kuyamika ndi Pemphero
Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani. Timayamika chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse. Chikhulupiriro ndi chikondi, gwero lake ndi chiyembekezo chomwe muli nacho chodzalandira zimene anakusungirani kumwamba. Munamva kale za zimenezi kudzera mʼmawu a choonadi, Uthenga Wabwino umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse. Inu munaphunzira zimenezi kuchokera kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwathu. Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani.
Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa. Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu. Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika. Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
Kupambana Koposa kwa Khristu
Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye. Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse. Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu. Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.
Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa. Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
Utumiki wa Paulo ku Mpingo
Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo. Ine ndakhala mtumiki wake mwa lamulo limene Mulungu anandipatsa kuti ndipereke Mawu a Mulungu athunthu, chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.
Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu. Ndi cholinga chimenechi, ine ndikugwira ntchito molimbika ndi mwamphamvu zonse zimene Iye anachita mwa ine.
Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso. Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso. Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.
Za Moyo Weniweni mwa Khristu
Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.
Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.
Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse. Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija. Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.
Ufulu Wathu
Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu. Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.
Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa: “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe. Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.
Moyo Watsopano
Tsono popeza munaukitsidwa pamodzi ndi Khristu, ikani mitima yanu pa zinthu za kumwamba, kumene Khristu akukhala ku dzanja lamanja la Mulungu. Muzifunafuna zinthu za kumwamba, osati zinthu za pa dziko lapansi. Pakuti munafa, ndipo moyo wanu tsopano wabisika pamodzi ndi Khristu mwa Mulungu. Khristu, amene ndiye moyo wanu, akadzaonekanso, pamenepo inunso mudzaoneka naye pamodzi mu ulemerero.
Choncho, iphani zilakolako za dziko lapansi mwa inu, monga: dama, zodetsa, kulakalaka zosayenera, kukhumba zoyipa ndi umbombo, pakuti umbombo ndiko kupembedza mafano. Chifukwa cha zimenezi, mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa ana osamvera. Inunso kale munkachita zomwezi, mʼmoyo wanu wakale uja. Koma tsopano mukuyenera kuzichotsa zinthu zonsezi monga: mkwiyo, ukali, dumbo, chipongwe ndi mawu onyansa. Musanamizane wina ndi mnzake, popeza munavula munthu wakale pamodzi ndi zochita zake ndipo mwavala munthu watsopano, amene nzeru zake zikukonzedwanso kuti afanane ndi Mlengi wake. Pano palibe kusiyana pakati pa Mgriki ndi Myuda, wochita mdulidwe ndi wosachita, wosaphunzira kapena wosachangamuka, kapolo kapena mfulu, koma Khristu yekha basi ndipo amakhala mwa onse.
Choncho, ngati anthu osankhidwa ndi Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa kwambiri, muvale chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, kufatsa ndi kupirira. Mulezerane mtima ndipo muzikhululukirana ngati wina ali ndi chifukwa ndi mnzake. Muzikhululukirana monga Ambuye anakhululukira inu. Ndipo kuwonjezera pa zonsezi valani chikondi, chimene chimangirira zonsezi pamodzi mu mgwirizano wangwiro.
Mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima mwanu, popeza monga ziwalo za thupi limodzi, munayitanidwa kuti mukhale ndi mtendere. Ndipo muziyamika. Mawu a Khristu akhazikike kwathunthu mʼmitima mwanu. Muziphunzitsana ndi kulangizana wina ndi mnzake ndi nzeru zonse pamene mukuyimba Masalimo, nyimbo zotamanda ndi nyimbo zauzimu, kuyimbira Mulungu ndi mitima yoyamika. Ndipo chilichonse chimene mungachite, kaya nʼkuyankhula, kaya nʼkugwira ntchito, muchite zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, kuyamika kwa Mulungu Atate kudzera mwa Iye.
Malangizo a Moyo wa Mʼbanja la Chikhristu
Inu akazi, gonjerani amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.
Inu amuna, kondani akazi anu ndipo musawapsere mtima.
Inu ana, mverani makolo anu mu zonse pakuti izi zimakondweretsa Ambuye.
Inu abambo, musakwiyitse ana anu, kuti angataye mtima.
Inu antchito, mverani mabwana anu mu zonse, ndipo muzichita zimenezi osati nthawi yokhayo imene akukuonani kuti akukondeni, koma muzichite moona mtima ndi mopereka ulemu kwa Ambuye. Chilichonse mungachite, muchite ndi mtima wanu onse, monga mmene mungagwirire ntchito ya Ambuye osati ya anthu. Inu mukudziwa kuti mudzalandira mphotho monga cholowa kuchokera kwa Ambuye. Ndi Ambuye Khristu amene mukumutumikira. Aliyense amene amachita zolakwa adzalandira malipiro molingana ndi kulakwa kwake, ndipo palibe tsankho.
Mabwana, antchito anu muzikhala nawo mwachilungamo ndi moyenera, podziwa kuti nanunso muli nawo Ambuye anu mmwamba.
Malangizo Ena
Pempherani modzipereka, mukhale atcheru ndiponso oyamika. Ndipo muzitipemphereranso ife kuti Mulungu atitsekulire khomo la uthenga wathu, kuti tilalikire chinsinsi cha Khristu, chimene ndine womangidwa nacho mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire momveka bwino, monga ndikuyenera. Mayendedwe anu pakati pa akunja, akhale anzeru ndipo mugwiritse ntchito mpata uliwonse umene muli nawo. Mayankhulidwe anu nthawi zonse akhale odzaza ndi chisomo ndi okoma, kuti mudziwe kuyankha aliyense.
Mawu Otsiriza
Tukiko adzakuwuzani zonse za ine. Iye ndi mʼbale wokondedwa, mtumiki wokhulupirika ndiponso wantchito mnzanga mwa Ambuye. Ine ndikumutumiza kwa inu ndi cholinga choti mudziwe zimene tikukumana nazo ndiponso kuti alimbikitse mitima yanu. Iye akubwera ndi Onesimo, mʼbale wathu wokhulupirika ndi wokondedwa, amene ndi mmodzi mwa inu. Iwo adzakuwuzani zonse zimene zikuchitika kuno.
Aristariko, wamʼndende mnzanga akupereka moni, Marko akuperekanso moni, msuweni wa Barnaba. (Inu munawuzidwa kale za Iye. Iye akabwera kwanuko, mulandireni). Yesu wotchedwa Yusto, akuperekanso moni. Amenewa ndi Ayuda okhawo pakati pa atumiki anzanga mu ufumu wa Mulungu, ndipo aonetsa kuti ndi chitonthozo kwa ine. Epafra ndi mmodzi mwa inu ndiponso mtumiki wa Khristu Yesu, akupereka moni. Iyeyu nthawi zonse amakupemphererani mwamphamvu, kuti mukhazikike pa chifuniro chonse cha Mulungu, mukhale okhwima ndi otsimikiza kwathunthu. Ine ndikumuchitira umboni kuti amagwira ntchito mwamphamvu chifukwa cha inu ndiponso kwa amene ali ku Laodikaya ndi Herapoli. Luka, dotolo wathu wokondedwa ndi Dema, akupereka moni. Perekani moni kwa abale a ku Laodikaya, ndiponso kwa Numfa ndi mpingo wa mʼnyumba mwake.
Kalata iyi ikawerengedwa pakati panu, muonetsetse kuti ikawerengedwenso ku mpingo wa ku Laodikaya ndipo inunso muwerenge kalata yochokera ku Laodikaya.
Uzani Arkipo kuti, “Wonetsetsa kuti wamaliza ntchito imene unayilandira mwa Ambuye.”
Ine Paulo, ndikulemba ndi dzanja langa moni uwu. Kumbukirani kuti ndili mu unyolo. Chisomo chikhale ndi inu.