- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 AMOSI Amosi Amosi Amo Amosi Mawu a Amosi, mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa. Zimene iye anaona mʼmasomphenya zokhudza Israeli patatsala zaka ziwiri kuti chivomerezi chichitike, nthawi imene Uziya anali mfumu ya Yuda ndipo Yeroboamu mwana wa Yowasi anali mfumu ya Israeli. Amosi anati: “Yehova akubangula mu Ziyoni ndipo akumveka ngati bingu mu Yerusalemu; msipu wa abusa ukulira, ndipo pamwamba pa Karimeli pakuwuma.” Chiweruzo pa Anthu Oyandikana ndi Israeli Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Damasiko akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anapuntha Giliyadi ndi zopunthira za mano achitsulo, Ine ndidzatumiza moto pa nyumba ya Hazaeli umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Beni-Hadadi. Ndidzathyola chipata cha Damasiko; ndidzawononga mfumu yokhala ku Chigwa cha Aveni, ndiponso iye amene akugwira ndodo yaufumu mu Beti-Edeni. Anthu a ku Aramu adzapita ku ukapolo ku Kiri,” akutero Yehova. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Gaza akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatenga ukapolo mtundu wathunthu ndi kuwugulitsa ku Edomu, ndidzatumiza moto pa makoma a Gaza umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu. Ndidzawononga mfumu ya ku Asidodi komanso amene akugwira ndodo yaufumu ku Asikeloni. Ndidzalanga Ekroni, mpaka wotsala mwa Afilisti atafa,” akutero Ambuye Yehova. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Turo akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo anagulitsa mtundu wathunthu ku ukapolo ku Edomu, osasunga pangano laubale lija, Ine ndidzatumiza moto pa makoma a Turo umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu.” Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Edomu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anathamangitsa mʼbale wake ndi lupanga, popanda nʼchifundo chomwe. Popeza mkwiyo wake unakulabe ndipo ukali wake sunatonthozeke, Ine ndidzatumiza moto pa Temani umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za Bozira.” Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Amoni akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatumbula akazi oyembekezera a ku Giliyadi nʼcholinga choti akuze malire awo, Ine ndidzayatsa moto pa makoma a ku Raba umene udzanyeketsa nyumba zake zaufumu. Padzakhala kulira kwakukulu pa tsiku la nkhondoyo, kumenyana kudzakhala kwafumbi ngati mkuntho wa kamvuluvulu. Mfumu yawo idzatengedwa kupita ku ukapolo, iyo pamodzi ndi akuluakulu ake,” akutero Yehova. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Mowabu akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu, mpaka kuwasandutsa phulusa, Ine ndidzatumiza moto pa Mowabu, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Keriyoti. Mowabu adzafera pakati pa nkhondo yoopsa, mʼkati mwa mfuwu wa nkhondo ndi kuliza malipenga. Ndidzawononga wolamulira wake ndi kupha akuluakulu onse amene ali pamodzi ndi iye,” akutero Yehova. Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Popeza iwo akana lamulo la Yehova ndipo sanasunge malangizo ake, popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza, milungu imene makolo awo ankayitsatira, Ine ndidzatumiza moto pa Yuda, umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.” Chilango cha Anthu a ku Israeli Yehova akuti, “Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira, Ine sindileka kuwalanga. Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva, ndi osauka ndi nsapato. Amapondereza anthu osauka ngati akuponda fumbi, ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa. Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo, ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera. Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe pa zovala zimene anatenga ngati chikole. Mʼnyumba ya mulungu wawo amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu. “Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo, ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu. Ndinawononga zipatso zawo ndiponso mizu yawo. “Ine ndinakutulutsani ku Igupto, ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi, kudzakupatsani dziko la Aamori. Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri, ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri. Kodi si choncho, inu Aisraeli?” akutero Yehova. “Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja, ndipo munalamula aneneri kuti asanenere. “Tsono Ine ndidzakupsinjani monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu. Munthu waliwiro sadzatha kuthawa, munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga, wankhondo sadzapulumutsa moyo wake. Munthu wa uta sadzalimbika, msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka, ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake. Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri adzathawa ali maliseche pa tsikulo,” akutero Yehova. Mboni Zotsutsa Israeli Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto: “Inu nokha ndi amene ndinakusankhani pakati pa mabanja onse a dziko lapansi; nʼchifukwa chake ndidzakulangani chifukwa cha machimo anu onse.” Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi asanapangane? Kodi mkango umabangula mʼnkhalango usanagwire nyama? Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake pamene sunagwire kanthu? Kodi mbalame nʼkutera pa msampha pamene palibe nyambo yake? Kodi msampha umafwamphuka usanakole kanthu? Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda, anthu sanjenjemera? Pamene tsoka lafika mu mzinda, kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo? Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu asanawulule zimene akufuna kuchita kwa atumiki ake, aneneri. Mkango wabangula, ndani amene sachita mantha? Ambuye Yehova wayankhula, ndani amene sanganenere? Lengezani zimenezi ku nyumba zaufumu za ku Asidodi ndiponso ku nyumba zaufumu za ku Igupto: “Sonkhanani ku mapiri a ku Samariya; onani chisokonezo pakati pake ndiponso kuponderezana pakati pa anthu ake.” “Iwo sadziwa kuchita zolungama, ndipo amadzaza malo awo otetezedwa ndi zinthu zolanda ku nkhondo ndi zakuba,” akutero Yehova. Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akunena izi: “Mdani adzalizungulira dzikoli; iye adzagwetsa malinga ako, ndi kufunkha nyumba zako zaufumu.” Yehova akuti, “Monga mʼbusa amalanditsa mʼkamwa mwa mkango miyendo iwiri yokha kapena msonga yokha ya khutu, moteronso ndimo mmene adzapulumukire Aisraeli amene amakhala mu Samariya pa msonga za mabedi awo, ndi ku Damasiko pa akakhutagona awo.” “Imvani izi ndipo mupereke umboni wotsutsa nyumba ya Yakobo,” akutero Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. “Pa tsiku limene ndidzalange Israeli chifukwa cha machimo ake, ndidzagumula maguwa ansembe a ku Beteli; nyanga za guwa zidzathyoka ndipo zidzagwa pansi. Ndidzagwetsa nyumba ya pa nthawi yozizira pamodzi ndi nyumba ya pa nthawi yotentha; nyumba zokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu zidzawonongedwa ndipo nyumba zikuluzikulu zidzaphwasulidwa,” akutero Yehova. Israeli Sanabwerere kwa Mulungu Imvani mawu awa, inu ngʼombe zazikazi za ku Basani, okhala pa Phiri la Samariya, inu akazi amene mumapondereza anthu osauka ndi kuzunza anthu osowa ndi kumanena kwa amuna anu kuti, “Tipatseni zakumwa!” Ambuye Yehova, mwa kuyera mtima kwake walumbira kuti, “Nthawi idzafika ndithu pamene adzakukokani ndi ngowe, womaliza wa inu adzakokedwa ndi mbedza. Mudzatulukira mʼmingʼalu ya pa khoma aliyense payekhapayekha, ndipo mudzatayidwa ku Harimoni,” akutero Yehova. “Bwerani ku Beteli mudzachimwe; ndi ku Giligala kuti mudzapitirize kuchimwa. Bweretsani nsembe zanu mmawa uliwonse, bweretsani chakhumi chanu masiku atatu aliwonse. Wotchani buledi wokhala ndi yisiti ngati nsembe yachiyamiko ndi kumanyadira poyera za zopereka zanu zaufulu. Inu Aisraeli, zinyadireni nsembezo, pakuti izi ndi zimene mumakonda kuchita,” akutero Ambuye Yehova. “Ndine amene ndinakusendetsani milomo mʼmizinda yanu yonse, ndipo munasowa chakudya mʼmizinda yanu. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova. “Ndinenso amene ndinamanga mvula patangotsala miyezi itatu kuti mukolole. Ndinagwetsa mvula pa mzinda wina, koma pa mzinda wina ayi, mvula inkagwa pa munda wina; koma sinagwe pa munda wina ndipo mbewu zinawuma. Anthu ankayenda mzinda ndi mzinda kufuna madzi, koma sanapeze madzi okwanira kumwa. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova. “Nthawi zambiri ndinakantha mbewu zanu ndiponso minda ya mpesa, ndinayikantha ndi chinsikwi ndiponso ndi chiwawu. Dzombe linawononga mikuyu yanu ndi mitengo ya olivi. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova. “Ine ndinabweretsa miliri pakati panu monga ndinachitira ku Igupto. Ndinapha anyamata anu ndi lupanga, ndinapereka akavalo anu kwa adani. Ndinakununkhitsani fungo la mitembo lochokera mʼmisasa yanu ya nkhondo. Komatu inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova. “Ndinawononga ena mwa inu monga ndinawonongera Sodomu ndi Gomora. Inu munali ngati chikuni choyaka chimene chafumulidwa pa moto. Komabe inu simunabwerere kwa Ine,” akutero Yehova. “Choncho izi ndi zimene ndidzakuchitire iwe Israeli, chifukwa ndidzakuchitira zimenezi, konzekera kukumana ndi Mulungu wako, iwe Israeli.” Iye amene amawumba mapiri, amalenga mphepo, ndipo amawululira munthu za mʼmaganizo ake, Iye amene amasandutsa usana kuti ukhale mdima, ndipo amayenda pa zitunda za dziko lapansi, dzina lake ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Mawu Odandawulira Aisraeli Israeli, imva mawu awa, nyimbo ya maliro imene ndikuyimba za iweyo: “Namwali Israeli wagwa, moti sadzadzukanso, wasiyidwa mʼdziko lake lomwe, popanda woti ndi kumudzutsa.” Ambuye Yehova akuti, “Mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 1,000 amphamvu udzatsala ndi anthu 100 okha; mzinda umene udzapite ku nkhondo ndi anthu 100 amphamvu udzatsala ndi anthu khumi okha basi.” Zimene Yehova akunena kwa nyumba ya Israeli ndi izi: “Mundifunefune kuti mukhale ndi moyo; musafunefune Beteli, musapite ku Giligala, musapite ku Beeriseba. Pakuti Giligala adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, ndipo Beteli adzawonongekeratu.” Funani Yehova kuti mukhale ndi moyo, mukapanda kutero Iye adzatentha nyumba ya Yosefe ngati moto; motowo udzawononga, ndipo sipadzakhala wina wozimitsa motowo ku Beteli. Inu amene mumasandutsa chiweruzo cholungama kukhala chowawa ndi kunyoza chilungamo. (Iye amene analenga nyenyezi za Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, amene amasandutsa mdima kuti ukhale mmawa ndi kudetsa usana kuti ukhale usiku, amene amayitana madzi a mʼnyanja ndi kuwathira pa dziko lapansi, Yehova ndiye dzina lake. Iyeyo amabweretsa chiwonongeko modzidzimutsa pa anthu amphamvu ndi kuwononga mizinda yotetezedwa), inu mumadana ndi amene amadzudzula mʼbwalo la milandu ndi kunyoza amene amanena zoona. Mumapondereza munthu wosauka ndi kumukakamiza kuti akupatseni tirigu. Nʼchifukwa chake, ngakhale mwamanga nyumba zamiyala yosema, inuyo simudzakhalamo. Ngakhale mwalima minda yabwino ya mphesa, inu simudzamwa vinyo wake. Pakuti Ine ndikudziwa kuchuluka kwa zolakwa zanu ndi kukula kwa machimo anu. Inu mumapondereza anthu olungama ndi kulandira ziphuphu ndipo anthu osauka simuwaweruza mwachilungamo mʼmabwalo anu amilandu. Nʼchifukwa chake pa nthawi yotere munthu wanzeru sayankhulapo kanthu, popeza ndi nthawi yoyipa. Muyike mtima wanu pa zabwino osati pa zoyipa, kuti mukhale ndi moyo. Mukatero Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzakhala nanu, monga mmene mumanenera kuti ali nanu. Mudane ndi zoyipa, mukonde zabwino; mukhazikitse chiweruzo cholungama mʼmabwalo anu amilandu. Mwina mwake Yehova Mulungu Wamphamvuzonse adzachitira chifundo anthu otsala a mʼbanja la Yosefe. Choncho izi ndi zimene Ambuye, Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, akunena: “Mʼmisewu monse mudzakhala kulira mofuwula, ndi kulira chifukwa cha kuwawa kwa masautso kudzakhala paliponse. Adzayitana alimi kuti adzalire, ndipo anthu odziwa maliridwe anthetemya adzalira mofuwula. Mʼminda yonse ya mpesa mudzakhala kulira kokhakokha, pakuti Ine ndidzadutsa pakati panu,” akutero Yehova. Tsiku la Yehova Tsoka kwa inu amene mumalakalaka tsiku la Yehova! Chifukwa chiyani mumalakalaka tsiku la Yehova? Tsikulo kudzakhala mdima osati kuwala. Lidzakhala ngati tsiku limene munthu pothawa mkango amakumana ndi chimbalangondo, ngati pamene munthu walowa mʼnyumba, natsamira dzanja lake pa khoma ndipo njoka nʼkuluma. Kodi tsiku la Yehova silidzakhala mdima osati kuwala, mdima wandiweyani, popanda powala pena paliponse? “Ndimadana nawo masiku anu achikondwerero ndipo ndimawanyoza; sindikondwera nayo misonkhano yanu. Ngakhale mupereke nsembe zopsereza ndi nsembe zachakudya, Ine sindidzazilandira. Ngakhale mupereke nsembe zabwino zachiyanjano, Ine sindidzaziyangʼana nʼkomwe. Musandisokose nazo nyimbo zanu! Sindidzamvetsera kulira kwa azeze anu. Koma chiweruzo cholungama chiyende ngati madzi, chilungamo ngati mtsinje wosaphwa! “Kodi pa zaka makumi anayi zimene munakhala mʼchipululu muja munkandibweretsera nsembe ndi zopereka, inu nyumba ya Israeli? Inu mwanyamula kachisi wa mfumu yanu, ndi nyenyezi ija Kaiwani, mulungu wanu, mafano amene munadzipangira. Nʼchifukwa chake Ine ndidzakupititsani ku ukapolo, kutali kupitirira ku Damasiko,” akutero Yehova, amene dzina lake ndi Mulungu Wamphamvuzonse. Tsoka kwa Osalabadira Kanthu Tsoka kwa amene simukulabadira kanthu ku Ziyoni, ndiponso kwa inu amene mukukhala mwamtendere pa Phiri la Samariya, inu anthu otchuka ochokera ku mtundu wa anthu omveka, kumene Aisraeli amafikako! Pitani ku mzinda wa Kaline mukawuyangʼane; mukapitenso ku Hamati-raba mzinda waukulu uja, ndipo mukatsikirenso ku Gati kwa Afilisti. Kodi mizinda imeneyi ndi yopambana maufumu anu awiriwa? Kodi dziko lawo ndi lalikulu kupambana lanu? Inu simulabadirako kuti tsiku loyipa lidzafika, zochita zanu zimafulumizitsa ulamuliro wankhanza. Mumagona pa mabedi owakongoletsa ndi minyanga ya njovu, mumagona pa mipando yanu ya wofuwofu. Mumadya ana ankhosa onona ndi ana angʼombe onenepa. Mumayimba azeze anu ndi kumangopeka nyimbo pa zingʼwenyengʼwenye ngati Davide. Mumamwera vinyo mʼzipanda zodzaza ndipo mumadzola mafuta abwino kwambiri, koma simumva chisoni ndi kuwonongeka kwa Yosefe. Nʼchifukwa chake inu mudzakhala mʼgulu la anthu oyamba kupita ku ukapolo; maphwando ndi zikondwerero zanu zidzatheratu. Yehova Amanyansidwa ndi Kunyada kwa Israeli Ambuye Yehova walumbira mʼdzina lake. Yehova Mulungu Wamphamvuzonse walengeza kuti, “Ndimanyansidwa ndi kunyada kwa Yakobo, ndimadana ndi nyumba zake zaufumu; Ine ndidzawupereka mzindawu pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo.” Ngati anthu khumi otsala adzabisala mʼnyumba imodzi, nawonso adzafa ndithu. Ndipo ngati mʼbale wake wa wina wakufayo, woyenera kusamala za maliro, adzafika kudzatulutsa mitembo mʼnyumbamo nʼkufunsa aliyense amene akubisalabe mʼnyumbamo kuti, “Kodi uli ndi wina wamoyo mʼmenemo?” Ndipo munthu wobisalayo ndi kuyankha kuti, “Ayi,” mʼbaleyo adzanena kuti, “Khala chete! Ife tisayerekeze kutchula dzina la Yehova.” Pakuti Yehova walamula kuti nyumba zikuluzikulu Iye adzazigamulagamula, ndipo nyumba zazingʼono zidzasanduka maduka okhaokha. Kodi akavalo amathamanga pa thanthwe? Kodi wina amatipula ndi ngʼombe mʼnyanja? Koma chiweruzo cholungama mwachisandutsa kukhala zinthu zakupha ndipo chipatso cha chilungamo mwachisandutsa kukhala chowawa. Inu amene mukunyadira kuti munagonjetsa Lo Debara ndipo mukunena kuti, “Kodi sitinatenge Karinaimu ndi mphamvu zathu zokha?” Koma Yehova Mulungu Wamphamvuzonse akulengeza kuti, “Inu nyumba ya Israeli, ndidzakudzutsirani mtundu wina wa anthu umene udzakuzunzani kuchokera ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha Araba.” Dzombe, Moto ndi Chingwe Chowongolera Khoma Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Yehova ankasonkhanitsa gulu la dzombe nthawi imene gawo la zokolola za mfumu linali litakololedwa kale ndipo mbewu zachiwiri zinali zitangoyamba kumera kumene. Dzombelo litadya zomera zonse za mʼdzikomo, Ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, khululukani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!” Kotero Yehova anakhululuka. Yehovayo anati, “Izi sizidzachitika.” Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: Ambuye Yehova ankayitana malawi a moto kuti alange anthu. Motowo unawumitsa nyanja yakuya ndi kupsereza dziko. Tsono ine ndinafuwula kuti, “Ambuye Yehova, chonde ndikukupemphani, lekani! Kodi Yakobo adzapulumuka bwanji? Iye ndi wofowoka kwambiri!” Kotero Yehova anakhululuka. Ambuye Yehova anati, “Izinso sizidzachitika.” Zimene Iye anandionetsa ndi izi: Ambuye anayima pambali pa khoma lomangamanga, mʼmanja mwake muli chingwe chowongolera khoma. Ndipo Ambuye anandifunsa kuti, “Amosi, nʼchiyani ukuonachi?” Ine ndinayankha kuti, “Chingwe chowongolera khoma.” Ndipo Yehova anati, “Taona, Ine ndikuyika chingwe chowongolerachi pakati pa anthu anga, Aisraeli; sindidzawalekereranso. “Malo achipembedzo a Isake adzawonongedwa ndipo malo opatulika a Israeli adzasanduka bwinja; ndidzagwetsa nyumba ya Yeroboamu ndi lupanga langa.” Amosi ndi Amaziya Pamenepo Amaziya wansembe wa ku Beteli anatumiza uthenga kwa Yeroboamu mfumu ya Israeli kuti, “Amosi akukuutsirani chiwembu pakati pa Aisraeli. Dziko silingalekerere zonena zake zonsezo. Pakuti zimene Amosi akunena ndi izi: “ ‘Yeroboamu adzaphedwa ndi lupanga, ndipo Israeli adzapita ndithu ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ” Ndipo Amaziya anawuza Amosi kuti, “Choka, mlosi iwe! Bwerera ku dziko la Yuda. Uzikalosera kumeneko ndipo anthu a kumeneko azikakudyetsa. Usanenerenso ku Beteli, chifukwa kumeneko ndi malo opatulika a mfumu ndiponso ndi malo a nyumba yachipembedzo yaufumu.” Amosi anayankha Amaziya kuti, “Ine sindine mneneri kapena mwana wa mneneri; koma ndine woweta ziweto, ndiponso mlimi wa nkhuyu. Koma Yehova ananditenga ndikuweta nkhosa ndipo anati, ‘Pita ukanenere kwa anthu anga Aisraeli.’ Tsono imva mawu a Yehova. Iwe ukunena kuti, “ ‘Usanenere zotsutsa Israeli, ndipo siya kulalikira motsutsa nyumba ya Isake.’ ” “Tsono zimene akunena Yehova ndi izi: “ ‘Mkazi wako adzasanduka wachiwerewere mu mzindamu, ndipo ana ako aamuna ndi aakazi adzaphedwa ndi lupanga. Munda wako udzayezedwa ndi chingwe ndi kugawidwa, ndipo iwe mwini udzafera mʼdziko la anthu osapembedza Mulungu. Ndipo Israeli adzatengedwa ndithu kupita ku ukapolo, kutali ndi dziko lake.’ ” Dengu la Zipatso Zakupsa Zimene Ambuye Yehova anandionetsa ndi izi: dengu la zipatso zakupsa. Iye anandifunsa kuti, “Amosi nʼchiyani ukuona?” Ine ndinayankha kuti, “Dengu la zipatso zakupsa.” Ndipo Yehova anati kwa ine, “Nthawi yachimaliziro yawakwanira anthu anga Aisraeli; sindidzawakhululukiranso. “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akulengeza kuti, “Nyimbo za mʼNyumba ya Mulungu zidzasanduka kulira kofuwula. Mitembo ya anthu idzachuluka, ndipo adzayiponya ponseponse! Kudzangoti zii!” Imvani izi, inu amene mumapondereza anthu osowa ndipo simulabadira anthu osauka a mʼdzikomu. Mumanena kuti, “Kodi chikondwerero cha mwezi watsopano chidzatha liti kuti tigulitse zinthu? Ndipo tsiku la Sabata litha liti kuti tigulitse tirigu, kuti tichepetse miyeso, kukweza mitengo kuti tibere anthu ndi miyeso ya chinyengo, tigule osauka ndi ndalama zasiliva ndi osowa powapatsa nsapato, tigulitse ngakhale mungu wa tirigu?” Yehova amene Yakobo amamunyadira, walumbira kuti: Ine sindidzayiwala chilichonse chimene anachita. “Kodi dziko silidzagwedezeka chifukwa cha zimenezi, ndi onse okhala mʼmenemo kulira mwachisoni? Dziko lonse lidzavunduka ngati mtsinje wa Nailo; lidzagwedezeka kenaka nʼkukhala bata ngati mtsinje wa ku Igupto. “Tsiku limenelo,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzadetsa dzuwa masana ndi kugwetsa mdima pa dziko lapansi dzuwa likuswa mtengo. Maphwando anu achipembedzo ndidzawasandutsa kulira kwa chisoni ndipo kuyimba kwanu konse ndidzakusandutsa maliro. Ndidzakuvekani chiguduli nonsenu ndi kumeta mipala mitu yanu. Nthawi imeneyo idzakhala ngati yolira mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ndipo tsikulo lidzakhala lowawa mpaka kutha kwake. “Nthawi ikubwera,” Ambuye Yehova akunena kuti, “Ndidzagwetsa njala mʼdziko lonse; osati njala ya chakudya kapena ludzu la madzi, koma njala yofuna kumva mawu a Yehova. Anthu azidzangoyendayenda kuchoka ku nyanja ina kupita ku nyanja ina. Azidzangoyendayenda kuchoka kumpoto kupita kummawa, kufunafuna mawu a Yehova, koma sadzawapeza. “Tsiku limenelo “anamwali okongola ndi anyamata amphamvu adzakomoka ndi ludzu. Onse amene amalumbira pa tchimo la Samariya, kapena kumanena kuti, ‘Iwe Dani, pali mulungu wako wamoyo,’ kapena, ‘Pali mulungu wamoyo wa ku Beeriseba.’ Iwowo adzagwa ndipo sadzadzukanso.” Israeli Adzawonongedwa Ine ndinaona Ambuye atayima pambali pa guwa lansembe, ndipo anati: “Kantha mitu ya nsanamira kuti ziwundo za nyumba zigwedezeke. Muzigwetsere pa mitu ya anthu onse, onse amene atsalira ndidzawapha ndi lupanga. Palibe ndi mmodzi yemwe amene adzathawe, palibe amene adzapulumuke. Ngakhale atakumba pansi mpaka ku malo a anthu akufa, dzanja langa lidzawatulutsa kumeneko. Ngakhale atakwera kumwamba Ine ndidzawatsakamutsa kumeneko. Ngakhale atakabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, Ine ndidzawasaka kumeneko ndi kuwagwira. Ngakhale atakabisala pansi pa nyanja yayikulu, ndidzalamula njoka kuti iwalume kumeneko. Ngakhale adani awo awakusire ku ukapolo, ndidzalamula lupanga kuti liwaphe kumeneko. Ndidzawayangʼanitsitsa kuti zoyipa ziwagwere; osati zabwino.” Ambuye Yehova Wamphamvuzonse amene amakhudza dziko lapansi ndipo dzikolo limasungunuka, onse amene amakhala mʼmenemo amalira. Dziko lonse lidzadzaza ngati mtsinje wa Nailo, kenaka nʼkuphwera ngati mtsinje wa ku Igupto. Iye amene amamanga malo ake okhalamo kumwamba, ndi kuyika maziko ake pa dziko lapansi, Iye amene amayitana madzi a ku nyanja ndikuwakhuthulira pa dziko lapansi, dzina lake ndiye Yehova. “Kodi kwa Ine, inu Aisraeli, simuli chimodzimodzi ndi Akusi?” Akutero Yehova. “Kodi sindine amene ndinatulutsa Israeli ku Igupto, Afilisti ku Kafitori ndi Aaramu ku Kiri? “Taonani, maso a Ambuye Yehova ali pa ufumu wochimwawu. Ndidzawufafaniza pa dziko lapansi. Komabe sindidzawononga kotheratu nyumba ya Yakobo,” akutero Yehova. “Pakuti ndidzalamula, ndipo ndidzagwedeza nyumba ya Israeli pakati pa mitundu yonse ya anthu monga momwe amasefera ufa mʼsefa, koma palibe nʼkamwala kamodzi komwe kamene kadzagwe pansi. Anthu onse ochimwa pakati pa anthu anga adzaphedwa ndi lupanga, onse amene amanena kuti, ‘Tsoka silidzatigwera ife kapena kutiwononga.’ Kubwezeretsedwa kwa Israeli “Tsiku limenelo ndidzabwezeretsa nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzakonzanso malo amene anagumuka, ndi kuyimanganso monga inalili poyamba, kuti adzatengenso otsala a Edomu ndi mitundu yonse imene imatchedwa ndi dzina langa,” akutero Yehova amene adzachita zinthu izi. Yehova akunena kuti “Nthawi ikubwera pamene mlimi wotipula adzapyola wokolola ndipo woponda mphesa adzapyola wodzala mbewu. Mapiri adzachucha vinyo watsopano ndi kuyenderera pa zitunda zonse. Ndidzawabwezeranso pabwino anthu anga Aisraeli; mizinda imene inali mabwinja idzamangidwanso ndipo azidzakhalamo. Adzalima minda ya mpesa ndipo adzamwa vinyo wake; adzalima minda ndipo adzadya zipatso zake. Ndidzakhazika Aisraeli mʼdziko mwawo, ndipo sadzachotsedwamonso mʼdziko limene Ine ndawapatsa,” akutero Yehova Mulungu wako.