- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 2 ATESALONIKA Kalata Yachiwiri ya Paulo Yolembera Atesalonika 2 Atesalonika 2 Ate KALATA YACHIWIRI YA PAULO YOLEMBERA ATESALONIKA Paulo, Silivano ndi Timoteyo. Kulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu. Chisomo ndi mtendere kwa inu kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. Kuyamika ndi Pemphero Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe. Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo. Zonsezi zikutsimikiza kuti Mulungu amaweruza molungama. Zotsatira zake ndi zakuti mudzatengedwa kukhala oyenera kulowa mu ufumu wa Mulungu umene mukuwuvutikira. Mulungu ndi wolungama ndipo adzalanga amene amakusautsaniwo ndikukupatsani mpumulo amene mukusautsidwa, pamodzi ndi ifenso. Izi zidzachitika Ambuye Yesu akadzaoneka mʼmalawi amoto kuchokera kumwamba pamodzi ndi angelo ake amphamvu. Iye adzalanga amene sadziwa Mulungu ndi amene samvera Uthenga Wabwino wa Ambuye athu Yesu. Adzalangidwa ndi chiwonongeko chamuyaya ndipo sadzaonanso nkhope ya Ambuye ndi ulemerero wamphamvu zake pa tsiku limene iye adzabwera kudzalemekezedwa mwa oyera mtima ndi kuyamikidwa ndi onse amene anakhulupirira. Inu mudzakhala nawo mʼgulumo chifukwa munakhulupirira umboni wathu. Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro. Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu. Kubwera kwa Munthu Woyipitsitsa Pa za kubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu ndiponso za kusonkhana kwathu kuti tikumane naye, abale, tikukupemphani kuti musagwedezeke msanga mʼmaganizo kapena kuopsezedwa ndi uneneri, mbiri kapena kalata yokhala ngati yachokera kwa ife, yonena kuti tsiku lija la Ambuye linafika kale. Musalole kuti wina aliyense akunamizeni mwa njira ina iliyonse. Pakuti tsikulo lisanafike, kudzakhala mpatuko waukulu kwambiri, ndipo kudzaoneka munthu woyipitsitsa uja, munthu woyenera kuwonongedwayo. Iyeyo adzatsutsa ndi kudziyika pamwamba pa chilichonse chimene anthu amachitcha mulungu kapena amachipembedza. Iyeyo adzadzikhazika mʼNyumba ya Mulungu ndi kudzitcha Mulungu. Kodi simukukumbukira kuti pamene ndinali nanu pamodzi ndinkakuwuzani zimenezi? Ndipo tsopano mukudziwa chimene chikumuletsa kuonekera, koma adzawululika pa nthawi yake yoyenera. Pakuti mphamvu yobisika yoyipitsitsa ikugwira ntchito ngakhale tsopano; koma amene akutchinga mphamvuyo adzapitiriza kutero mpaka pamene wotchingayo adzachotsedwe. Ndipo kenaka woyipitsitsayo adzaonekera, amene Ambuye Yesu adzamugonjetsa ndi mpweya otuluka mʼkamwa mwake ndi kumuwononga ndi ulemerero wa kubwera kwake. Woyipitsitsayo adzabwera ndi mphamvu za Satana. Adzaonetsa mphamvu zake pochita zizindikiro ndi zodabwitsa zachinyengo. Iye adzagwiritsa ntchito mtundu uliwonse wachinyengo kupusitsa amene akuwonongeka. Iwo akuwonongeka chifukwa akukana kukonda choonadi ndi kuti apulumutsidwe. Chifukwa cha chimenechi, Mulungu akuwatumizira chinyengo chachikulu kuti akhulupirire bodza. Choncho adzalangidwa onse amene sanakhulupirire choonadi, koma anakondwera mu zoyipa. Imani Mwamphamvu Koma tiyenera kuyamika Mulungu chifukwa cha inu abale okondedwa mwa Ambuye, pakuti Mulungu anakusankhani pachiyambi pomwe kuti mupulumuke chifukwa cha ntchito yoyeretsa ya Mzimu ndi chikhulupiriro chanu mʼchoonadi. Iye anakuyitanirani zimenezi kudzera mwa uthenga wathu wabwino, kuti mulandire nawo ulemerero wa Ambuye athu Yesu Khristu. Kotero tsono, abale, imani mwamphamvu ndi kugwiritsa ziphunzitso zimene tinakupatsani kudzera mʼmawu apakamwa kapena kudzera mʼkalata. Ambuye athu Yesu Khristu mwini ndi Mulungu Atate wathu, amene anatikonda ife ndipo mwachisomo chake anatipatsa kulimba mtima kwamuyaya ndi chiyembekezo chabwino, akulimbikitseni ndi kukupatsani mphamvu yogwirira ntchito ndi kuyankhula zabwino zilizonse. Tipempherereni Potsiriza, abale, mutipempherere kuti uthenga wa Ambuye ufalikire msanga ndi kulemekezedwa monga momwe munachitira inu. Ndipo pempherani kuti tilanditsidwe mʼmanja mwa anthu ovuta ndi oyipa, pakuti si onse amene ali nacho chikhulupiriro. Koma Ambuye ndi wokhulupirika, ndipo adzakulimbikitsani ndi kukutetezani kwa woyipayo. Tili ndi chikhulupiriro mwa Ambuye kuti mukuchita zonse ndipo mudzapitirira kuchita zimene tinakulamulirani. Ambuye atsogolere mitima yanu kuti mudziwe chikondi cha Mulungu ndiponso kupirira kumene Khristu amapereka. Awachenjeza za Kusagwira Ntchito Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.” Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino. Ngati wina aliyense akana kumvera malangizo athu a mʼkalatayi, mumuonetsetse ameneyo ndipo musayanjane naye kuti achite manyazi. Komatu musamutenge kukhala mdani, koma muchenjezeni ngati mʼbale. Malonje Otsiriza Tsopano Ambuye mwini mtendere akupatseni mtendere nthawi zonse mwa njira iliyonse. Ambuye akhale ndi inu nonse. Ine Paulo, ndikulemba malonje awa ndi dzanja langa, chimene ndi chizindikiro chodziwika mʼmakalata anga onse. Umo ndi mmene ndimalembera. Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale ndi inu nonse.