- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 2 SAMUELI 2 Samueli 2 Samueli 2 Sam 2 Samueli Davide Amva za Imfa ya Sauli Atamwalira Sauli, Davide anabwerako kumene anakagonjetsa Aamaleki ndipo anakakhala ku Zikilagi masiku awiri. Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo. Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.” Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?” Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.” Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?” Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira. Pamene anatembenuka ndi kundiona ine, iye anandiyitana, ndipo ndinati, ‘Kodi ndichite chiyani?’ ” Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?” Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.” “Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’ “Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.” Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo. Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga. Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa uthengawo, “Iwe umachokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine mwana wa mlendo Mwamaleki.” Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?” Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa. Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’ ” Davide Alira Maliro a Sauli ndi Yonatani Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani. Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari: “Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda. Taonani amphamvu agwa kumeneko! “Musakanene zimenezi ku Gati, musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni, kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale, ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere. “Inu mapiri a ku Gilibowa, musakhalenso ndi mame kapena mvula, kapena minda yobereka zopereka za ufa. Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa, chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta. “Pa magazi a ophedwa, pa mnofu wa amphamvu, uta wa Yonatani sunabwerere, lupanga la Sauli silinabwere chabe. “Sauli ndi Yonatani, pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima, ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe. Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga, anali ndi mphamvu zoposa mkango. “Inu ana aakazi a Israeli, mulireni Sauli, amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa, amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide. “Taonani amphamvu agwa ku nkhondo! Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda. Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani, unali wokondedwa kwambiri kwa ine. Chikondi chako pa ine chinali chopambana, chopambana kuposa chikondi cha akazi. “Taonani amphamvu agwa! Zida zankhondo zawonongeka!” Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Yuda Patapita nthawi, Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ku umodzi mwa mizinda ya Yuda?” Yehova anayankha kuti, “Pita.” Davide anafunsanso kuti, “Kodi ndipite kuti?” Yehova anayankha kuti, “Ku Hebroni.” Choncho Davide anapita kumeneko ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wamasiye uja wa Nabala wa ku Karimeli. Davide anatenganso anthu amene anali nawo aliyense ndi banja lake, ndipo anakakhala ku midzi ya ku Hebroni. Kenaka amuna a ku Yuda anabwera ku Hebroni ndipo kumeneko anadzoza Davide kukhala mfumu ya fuko la Yuda. Davide atawuzidwa kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi ndi amene anayika mʼmanda Sauli, iye anatuma amithenga kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti akayankhule nawo kuti, “Yehova akudalitseni poonetsa kukoma mtima kwanu kwa Sauli mbuye wanu pomuyika mʼmanda. Tsopano Yehova akuonetseni kukoma mtima ndi kukhulupirika kwake ndipo inenso ndidzakukomerani mtima chifukwa munachita zimenezi. Tsopano khalani amphamvu ndi olimba mtima, pakuti Sauli mbuye wanu wafa, ndipo fuko la Yuda landidzoza kukhala mfumu yawo.” Nkhondo Pakati pa Otsatira Davide ndi Otsatira Sauli Pa nthawi imeneyi Abineri mwana wa Neri, wolamulira ankhondo a Sauli, anatenga Isi-Boseti mwana wa Sauli ndi kubwera naye ku Mahanaimu. Iye anamuyika kuti akhale mfumu yoyangʼanira Giliyadi, Asuri ndi Yezireeli, pamodzi ndi Efereimu, Benjamini ndi Israeli yense. Isi-Boseti mwana wa Sauli anali wa zaka makumi anayi pamene anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira zaka ziwiri. Koma fuko la Yuda linatsatira Davide. Davide anakhala mfumu ku Hebroni akulamulira fuko la Yuda, kwa zaka zisanu ndi chimodzi ndi miyezi isanu ndi umodzi. Abineri mwana wa Neri, pamodzi ndi ankhondo a Isi-Boseti mwana wa Sauli, anachoka ku Mahanaimu ndi kupita ku Gibiyoni. Yowabu mwana wa Zeruya pamodzi ndi ankhondo a Davide anapita ndi kukakumana nawo ku dziwe la ku Gibiyoni. Gulu lina linakhala mbali ina ya dziwelo pamene gulu lina linakhala mbali inayo. Kenaka Abineri anati kwa Yowabu, “Tiye tibweretse ena mwa anyamata athu kuti amenyane patsogolo pathupa.” Yowabu anayankha, “Chabwino, amenyane.” Kotero anayimirira ndipo anawawerenga: anyamata khumi ndi awiri a fuko la Benjamini ndi Isi-Boseti mwana wa Sauli ndiponso anyamata khumi ndi awiri a Davide. Tsono aliyense anagwira mutu wa mnzake namubaya mnzakeyo mʼnthiti ndi mpeni ndipo onse anagwera pansi limodzi. Kotero malo amenewo ku Gibiyoni amatchedwa Helikati Hazurimu. Tsiku limeneli nkhondo yake inali yoopsa kwambiri, ndipo Abineri ndi ankhondo a Israeli anagonjetsedwa ndi ankhondo a Davide. Ana atatu aamuna a Zeruya, Yowabu, Abisai ndi Asaheli anali komweko. Koma Asaheli anali waliwiro ngati insa. Iye anathamangitsa Abineri ndipo sanakhotere kumanja kapena kumanzere pamene amamutsatira. Abineri anayangʼana mʼmbuyo ndipo anafunsa, “Kodi ndiwe Asaheli?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Ndipo Abineri anati kwa iye, “Khotera kumanja kapena kumanzere: tsatira mmodzi mwa anyamatawa ndipo umulande zida zake.” Koma Asaheli sanasiye kumuthamangitsa. Abineri anamuchenjezanso Asaheli, “Siya kuthamangitsa ine! Kodi ndikukanthe chifukwa chiyani? Kodi ndikaonana naye bwanji mʼbale wako Yowabu?” Koma iye anakana kuleka kumuthamangitsa. Choncho Abineri anabaya Asaheli mʼmimba ndi msonga ya mkondo wake ndipo mkondowo unatulukira mbali ina. Iye anagwa ndi kufera pamalo pomwepo. Ndipo munthu aliyense amayima akafika pamalo pamene anagwera ndi kufa. Koma Yowabu ndi Abisai anathamangitsa Abineri, ndipo dzuwa likulowa, anafika ku phiri la Ama, pafupi ndi Giya pa njira yopita ku chipululu cha ku Gibiyoni. Pamenepo anthu a fuko la Benjamini anasonkhana kudzathandiza Abineri. Iwo anapanga gulu ndipo anayima pamwamba pa phiri. Abineri anayitana Yowabu, “Kodi tipitirize kumenyana mpaka kalekale? Kodi sukuzindikira kuti mathero ake kudzakhala kuwawidwa mitima? Kodi udzawaletsa liti ankhondo ako kuthamangitsa abale awo?” Yowabu anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, ukanapanda kuyankhula, ankhondo anga akanapitiriza kuthamangitsa abale awo mpaka mmawa.” Chomwecho Yowabu analiza lipenga, ndipo ankhondo onse anayima. Iwo analeka kuthamangitsa Aisraeli kapena kumenyana nawo. Usiku wonsewo Abineri ndi ankhondo ake anayenda kudutsa Araba. Iwo anawoloka Yorodani, napitirira mpaka kudutsa dera lonse la Bitironi ndipo anafika ku Mahanaimu. Choncho Yowabu anabwerera kuchokera kothamangitsa Abineri ndipo anasonkhanitsa ankhondo ake onse. Kupatula Asaheli, panali ankhondo khumi ndi anayi a Davide amene anasowa. Koma ankhondo a Davide anapha ankhondo a fuko la Benjamini 360 amene anali ndi Abineri. Iwo anatenga Asaheli ndi kukamuyika mʼmanda a abambo ake ku Betelehemu. Ndipo Yowabu ndi ankhondo ake anayenda usiku wonse ndi kufika ku Hebroni kukucha. Nkhondo ya pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide inachitika nthawi yayitali. Mphamvu za Davide zinkakulirakulirabe, pamene banja la Sauli mphamvu zake zimapita zicheperachepera. Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli. Mwana wachiwiri anali Kileabu, amayi ake anali Abigayeli mkazi wamasiye wa Nabala wa ku Karimeli. Wachitatu anali Abisalomu, amayi ake anali Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; wachinayi anali Adoniya, amayi ake anali Hagiti; wachisanu, Sefatiya amayi ake anali Abitali; ndipo wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila, mkazi wa Davide. Ana awa a Davide anabadwira ku Hebroni. Abineri Agwirizana ndi Davide Pamene kunali nkhondo pakati pa banja la Sauli ndi banja la Davide, Abineri anayamba kudzipatsa yekha mphamvu pakati pa banja la Sauli. Sauli anali ndi mzikazi dzina lake Rizipa mwana wa Ayiwa. Ndipo Isiboseti anati kwa Abineri, “Nʼchifukwa chiyani unagona ndi mzikazi wa abambo anga?” Abineri anakwiya kwambiri chifukwa cha zimene Isi-Boseti ananena ndipo anamuyankha kuti “Kodi ukuyesa ndine mutu wagalu umene ali mbali ya Ayuda? Lero lino ndine wokhulupirika ku nyumba ya abambo ako, Sauli ndi banja lake ndi anzake. Ine sindinakupereke kwa Davide, koma tsopano ukundinena pa cholakwa chimene ndachita pa mkazi uyu! Mulungu andilange ine Abineri, andilange kwambiri, ngati sindichitira Davide zimene Yehova anamulonjeza iye mwa lumbiro. Ndidzachotsa ufumu ku nyumba ya Sauli ndi kukhazikitsa ufumu wa Davide pa Aisraeli onse ndi Yuda kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba.” Isiboseti sanayerekezenso kunena mawu ena kwa Abineri, chifukwa ankamuopa. Kenaka Abineri anatuma amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Kodi dzikoli ndi la yani? Uchite mgwirizano ndi ine ndipo ndidzakuthandiza kuti Aisraeli onse azikutsatira.” Davide anati, “Chabwino. Ine ndichita mgwirizano ndi iwe. Koma ndikukupempha chinthu chimodzi: Usabwere pamaso panga pokhapokha utabweretsa Mikala mwana wamkazi wa Sauli, ukamabwera kudzandiona.” Ndipo Davide anatuma amithenga kwa Isi-Boseti mwana wa Sauli, kumulamula kuti, “Patse mkazi wanga Mikala, amene ndinamukwatira ndi makungu 100 a msonga za mavalo a Afilisti.” Kotero Isi-Boseti analamulira ndipo anakamutenga kwa mwamuna wake Palitieli mwana wa Laisi. Koma mwamuna wake anapita naye akulira pambuyo pake njira yonse mpaka ku Bahurimu. Kenaka Abineri anati kwa iye, “Bwerera kwanu!” Ndipo anabwerera kwawo. Abineri anakambirana ndi akuluakulu a Israeli ndipo anati, “Kwa kanthawi mwakhala mukufuna kulonga Davide kuti akhale mfumu yanu. Tsopano chitani zimenezo! Pakuti Yehova analonjeza Davide kuti, ‘Kudzera mwa mtumiki wanga Davide ndidzapulumutsa anthu anga Aisraeli mʼdzanja la Afilisti ndi kuwachotsa mʼmanja mwa adani awo.’ ” Abineri anayankhulanso nawo yekha anthu a fuko la Benjamini. Kenaka anapita ku Hebroni kukamuwuza Davide zonse zimene Aisraeli ndi fuko lonse la Benjamini amafuna kuchita. Abineri, amene anali ndi anthu makumi awiri, atafika kwa Davide ku Hebroni, Davide anamukonzera phwando pamodzi ndi anthu ake. Ndipo Abineri anawuza Davide kuti, “Loleni kuti ndipite msanga kukasonkhanitsa Aisraeli onse kuti abwere kwa inu kuno, mbuye wanga mfumu, kuti adzachite nanu pangano, ndipo kuti muzilamulira kulikonse kumene mtima wanu ufuna.” Kotero Davide analola Abineri kuti apite, ndipo anapita mwamtendere. Yowabu Apha Abineri Nthawi yomweyo ankhondo a Davide ndi Yowabu anafika kuchokera kumene anakathira nkhondo ndipo anabweretsa katundu wambiri wolanda ku nkhondo. Koma Abineri sanalinso ndi Davide ku Hebroni, chifukwa Davide anamulola kuti apite, ndipo anapita mu mtendere. Yowabu ndi asilikali onse amene anali naye atafika, anawuzidwa kuti Abineri mwana wa Neri anabwera kwa mfumu ndipo kuti mfumu yamulola kuti apite ndi kuti wapita ndi mtendere. Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Mwachita chiyani? Taonani, Abineri anabwera kwa inu. Nʼchifukwa chiyani mwamulola kuti apite? Tsopanotu wapitadi! Inu mukumudziwa bwino Abineri mwana wa Neri. Iye anabwera kudzakunamizani ndi kudzaona mayendedwe anu ndiponso kudzaona zonse zimene mukuchita.” Kenaka Yowabu anachoka pamaso pa Davide ndipo anatumiza amithenga kutsatira Abineri, ndipo anabwera naye kuchokera ku chitsime cha Sira. Koma Davide sanadziwe zimenezi. Tsono Abineri atabwerera ku Hebroni, Yowabu anamutengera pambali ku chipata, kukhala ngati akufuna kuyankhula naye mwamseri. Ndipo kumeneko pobwezera imfa ya mʼbale wake Asaheli, Yowabu analasa iyeyo mʼmimba, ndipo anafa. Patapita nthawi, Davide atamva zimenezi anati, “Ine ndi ufumu wanga tidzakhala osalakwa pamaso pa Yehova pa imfa ya Abineri mwana wa Neri. Mlandu umenewu ukhala pa Yowabu ndi banja lonse la abambo ake! Mʼbanja la Yowabu musadzasowe munthu wodwala matenda a chizonono kapena khate, kapena wolumala woyendera ndodo kapena wophedwa ndi lupanga, kapena wosowa chakudya.” (Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anapha Abineri chifukwa iye anapha mʼbale wawo Asaheli ku nkhondo ku Gibiyoni). Ndipo Davide anati kwa Yowabu ndi anthu onse amene anali nawo, “Ngʼambani zovala zanu ndipo muvale ziguduli, muyende mukulira patsogolo pa Abineri.” Mfumu Davide mwini anayenda motsatira chitandacho. Iwo anamuyika Abineri mʼmanda ku Hebroni ndipo mfumu inalira mokweza pa manda a Abineri. Ndipo anthu onse analiranso. Mfumu inayimba nyimbo iyi ya maliro a Abineri: “Abineri nʼkufa motere monga mmene chimafera chitsiru. Manja ako anali osamanga, mapazi ako anali osakulungidwa. Iwe wafa monga mmene amafera anthu pamaso pa anthu oyipa.” Ndipo anthu onse analiranso kulirira Abineri. Kenaka onse anabwera kwa Davide kumuwumiriza kuti adye kusanade. Koma Davide analumbira kuti, “Mulungu andilange ine, andilange kwambiri, ngati ndilawe buledi kapena chilichonse dzuwa lisanalowe!” Anthu onse anadziwa zimenezi ndipo zinawakondweretsa ndithu. Zonse zimene mfumu inachita zinawakondweretsa. Kotero tsiku limeneli anthu onse ndi Aisraeli onse anadziwa kuti sikunali kufuna kwa mfumu kuti Abineri mwana wa Neri aphedwe. Ndipo mfumu inati kwa ankhondo ake, “Kodi inu simukudziwa kuti lero mu Israeli mwagwa kalonga ndi munthu wamkulu? Ndipo lero, ngakhale ine ndine mfumu yodzozedwa, ndilibe mphamvu ndipo ana awa a Zeruya ndi amphamvu kwa ine. Yehova abwezere woyipa molingana ndi zoyipa zake!” Kuphedwa kwa Isiboseti Isiboseti mwana wa Sauli atamva kuti Abineri waphedwa ku Hebroni, anataya mtima ndipo Aisraeli onse anachita mantha kwambiri. Koma Isiboseti anali ndi anthu akuluakulu awiri amene ankatsogolera magulu a ankhondo. Mmodzi mwa iwo dzina lake linali Baana ndipo mnzakeyo anali Rekabu. Iwo anali ana a Rimoni wa banja la Beeroti wa fuko la Benjamini Beeroti. Iwo ankatengedwa ngati mbali imodzi ya Benjamini, chifukwa anthu a ku Beeroti anathawira ku Gitaimu ndipo akhala ali kumeneko ngati alendo mpaka lero lino. (Yonatani mwana wa Sauli anali ndi mwana wamwamuna amene anali wolumala mapazi ake onse awiri. Iye anali ndi zaka zisanu pamene nkhani ya Sauli ndi Yonatani inamveka kuchokera ku Yezireeli. Amene amamulera anamunyamula ndi kuthawa naye, koma pamene amachita zinthu mofulumira mwanayo anagwa ndipo analumala. Dzina lake linali Mefiboseti). Choncho Rekabu ndi Baana ana a Rimoni wa ku Beeroti ananyamuka kupita ku nyumba ya Isi-Boseti, ndipo anafika nthawi ya masana kukutentha pamene iye amapumula. Iwo analowa mʼchipinda chamʼkati ngati kuti amakatenga tirigu, ndipo anamulasa mʼmimba. Kenaka Rekabu ndi mʼbale wake Baana anathawa. Iwo analowa mʼnyumbamo iye akugona pa bedi mʼchipinda chake. Atamulasa ndi kumupha, anadula mutu wake nʼkuwutenga, nayenda usiku wonse mʼnjira yopita ku Araba. Iwo anabweretsa mutu wa Isi-Boseti kwa Davide ku Hebroni ndipo anati kwa mfumu, “Nawu mutu wa Isiboseti mwana wa Sauli, mdani wanu, amene anafuna kukuphani. Lero lino Yehova wabwezera mbuye wanga mfumu adani anu, Sauli ndi ana ake.” Davide anayankha Rekabu ndi mʼbale wake Baana, ana a Rimoni wa ku Beeroti kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene wandipulumutsa ku mavuto anga onse, pamene munthu wina anandiwuza kuti, ‘Sauli wafa’ ndipo ankaganiza kuti wabweretsa nkhani yabwino, ine ndinamugwira ndi kumupha ku Zikilagi. Iyi inali mphotho imene ndinapereka kwa iyeyo chifukwa cha uthenga wake! Nanji pamene anthu oyipa apha munthu wosalakwa ali mʼnyumba mwake ndiponso pa bedi lake! Kodi ine ndingaleke kukulangani ndi kukuchotsani pa dziko lapansi pano?” Kotero Davide analamulira ankhondo ake, ndipo anawapha. Iwo anawadula manja ndi mapazi ndi kupachika matupi awo pa dziwe la ku Hebroni. Koma anatenga mutu wa Isi-Boseti nawuyika mʼmanda a Abineri ku Hebroni. Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli Mafuko onse a Israeli anabwera kwa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife mafupa ndi mnofu wanu. Kale lija, pamene Sauli anali mfumu yathu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova anakuwuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ” Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, mfumu inachita nawo pangano ku Hebroni pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli. Davide anali ndi zaka makumi atatu pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka makumi anayi. Analamulira Yuda ali ku Hebroni kwa zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi, ndipo ali ku Yerusalemu analamulira Israeli yense ndi Yuda kwa zaka 33. Davide Alanda Mzinda wa Yerusalemu Mfumu ndi ankhondo ake anapita ku Yerusalemu kukathira nkhondo Ayebusi amene ankakhala kumeneko. Ayebusiwo anamuwuza Davide kuti, “Inu simulowa muno. Ngakhale osaona ndi olumala akhoza kukuthamangitsani.” Iwo ankaganiza kuti, “Davide sangathe kulowa momwemo.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide. Pa tsiku limenelo Davide anati, “Aliyense wogonjetsa Ayebusi ayenera kudzera mʼngalande ya madzi kuti akafike kwa iwo amene ndi ‘olumala ndi osaona,’ amene ndi adani a Davide.” Nʼchifukwa chake amanena kuti, “Olumala ndi osaona sadzalowa mʼnyumba yaufumu.” Tsono Davide anakhazikika mu lingamo ndipo mzindawu anawutcha, Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Tsono Hiramu mfumu ya Turo inatumiza amithenga ake kwa Davide, pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndi amisiri a matabwa ndi amisiri a miyala, ndipo anamumangira Davide nyumba yaufumu. Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli. Davide atafika ku Yerusalemu kuchokera ku Hebroni, anakwatira azikazi natenganso akazi ena kumeneko, ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. Mayina a ana amene anabereka ku Yerusalemu ndi awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, Ibihari, Elisua, Nefegi, Yafiya, Elisama, Eliada ndi Elifeleti. Davide Agonjetsa Afilisti Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anakalowa mu linga. Ndipo Afilisti anabwera ndi kukhala momwazika mʼChigwa cha Refaimu. Davide anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka ndithu mʼmanja mwako.” Choncho Davide anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Yehova waphwanya adani anga ine ndikuona.” Choncho anawatcha malowa Baala Perazimu. Afilisti anasiya mafano awo kumeneko ndipo Davide ndi ankhondo ake anawatenga. Nthawi inanso Afilisti anabweranso namwazikana mʼChigwa cha Refaimu; Davide anafunsa Yehova ndipo Yehovayo anayankha kuti, “Usapite molunjika koma uzungulire kumbuyo kwawo ndipo ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukayende mofulumira, chifukwa izi zikasonyeza kuti Yehova ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” Kotero Davide anachita zimene Yehova anamulamulira ndipo anakantha Afilisti njira yonse kuchokera ku Geba mpaka ku Gezeri. Bokosi la Chipangano Libwera ku Yerusalemu Davide anasonkhanitsanso pamodzi ankhondo 3,000 osankhidwa pakati pa Aisraeli. Iye pamodzi ndi ankhondo ake onse anapita ku Baalahi ku Yuda kukatenga Bokosi la Chipangano la Mulungu, limene limadziwika ndi Dzina lake, dzina la Yehova Wamphamvuzonse, amene amakhala pakati pa Akerubi amene ali pa Bokosi la Chipanganolo. Iwo anayika Bokosi la Mulungu pa ngolo yatsopano nachoka nalo ku nyumba ya Abinadabu, imene inali pa phiri. Uza ndi Ahiyo ana a Abinadabu ndiwo ankayendetsa ngolo yatsopanoyo, imene inanyamula Bokosi la Mulungu, ndipo Ahiyo mwana wa Abinadabu ankayenda patsogolo pake. Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Yehova poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga. Atafika pa malo opunthira tirigu a Nakoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire Bokosi la Mulungu, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. Yehova anapsera mtima Uza chifukwa chochita chinthu chosayenera kuchitika. Choncho Mulungu anamukantha ndipo anafera pomwepo pambali pa Bokosi la Mulungulo. Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza. Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Yehova ndipo anati, “Kodi Bokosi la Yehova lingafike bwanji kwathu?” Iye sanafunenso kubwera ndi Bokosi la Yehova kawo ku mzinda wake wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. Bokosi la Yehova linakhala mʼnyumba ya Obedi-Edomu Mgiti kwa miyezi itatu, ndipo Yehova anamudalitsa kwambiri iyeyo ndi banja lake lonse. Tsono Mfumu Davide anawuzidwa kuti, “Yehova wadalitsa nyumba ya Obedi-Edomu ndi zonse zimene ali nazo, chifukwa cha Bokosi la Mulungu.” Choncho Davide anapita kukatenga Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Obedi-Edomu ndi kupita nalo ku mzinda wa Davide akukondwera kwambiri. Anthu amene ananyamula Bokosi la Yehova ankati akayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye ankapereka nsembe ngʼombe yayimuna ndi mwana wangʼombe wonenepa. Davide ankavina ndi mphamvu zake zonse pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala, pamene iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse ankabwera ndi Bokosi la Yehova, akufuwula ndi kuyimba malipenga. Bokosi la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikulumpha ndi kuvina pamaso pa Yehova, ankamunyogodola mu mtima mwake. Iwo anabwera nalo Bokosi la Yehova ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo Davideyo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova. Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse. Kenaka iye anagawira Aisraeli onsewo, aamuna ndi aakazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama, ndiponso keke yamphesa zowuma. Ndipo anthu onse anachokapo, napita aliyense ku nyumba kwake. Davide atabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake, Mikala mwana wamkazi wa Sauli anatuluka kudzakumana naye ndipo anati, “Kodi mfumu ya Israeli ingatero kudzilemekeza kwake lero, kudzithyolathyola pamaso pa akapolo aakazi, antchito ake ngati munthu wamba.” Davide anamuyankha Mikala kuti, “Ndachita zimenezi molemekeza Yehova, amene anandisankha ine kupambana abambo ako, kapenanso kupambana banja la abambo ako. Ndipo anandisankha kuti ndikhale wolamulira Aisraeli, anthu a Yehova. Nʼchifukwa chake ndidzasangalalabe pamaso pa Yehova. Ineyo ndidzadzinyoza kuposa apa, ndipo ndidzakhala wonyozeka mʼmaso mwako. Koma pakati pa akapolo aakazi awa amene umanena za iwo, ndidzalemekezedwa.” Ndipo Mikala mwana wa Sauli sanakhalenso ndi mwana mpaka anamwalira. Lonjezo la Mulungu kwa Davide Mfumu itakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, Yehova atayipatsa mpumulo kwa adani ake onse woyizungulira, mfumuyo inawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Mulungu lili mu tenti.” Natani anayankha mfumu kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu chifukwa Yehova ali nanu.” Usiku umenewo mawu a Yehova anafika kwa Natani ndipo anati, “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti: kodi ndiwe amene udzandimangira Ine nyumba yokhalamo? Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Aisraeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda uku ndi uku ndipo mokhala mwanga munali mu tenti. Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense atsogoleri awo, amene ndinamulamula kuweta anthu anga Aisraeli kuti, nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ” “Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse akuti: Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja, monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzakupatsaninso mpumulo kwa adani anu onse. “ ‘Yehova akulengeza kwa iwe kuti Iye mwini adzakhazikitsa banja lako: Masiku ako akadzatha ndipo ukadzakapuma ndi makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, imene idzachokera mʼthupi mwako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. Iye ndiye amene adzamangire nyumba Dzina langa, ndipo Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Akadzachita choyipa, Ineyo ndidzamulanga ndi ndodo ndi zikwapu za anthu. Koma sindidzasiya kumukonda, monga ndinachitira ndi Sauli, amene ndinamuchotsa iwe usanakhale mfumu. Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhala zamuyaya pamaso panga. Mpando wako waufumu udzakhazikika kwamuyaya!’ ” Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira. Pemphero la Davide Choncho Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati: “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ine ndine yani, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa?” Ndipo kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse, mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Kodi umu ndi mmene mumachitira ndi munthu, Inu Ambuye Wamphamvuzonse? Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu? Pakuti Inu Ambuye Wamphamvuzonse mukumudziwa mtumiki wanu. Chifukwa cha mawu anu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwachiwulula kwa mtumiki wanu. Inu ndinu wamkulu, Yehova Wamphamvuzonse! Palibe wina wofanana nanu, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha, monga tamvera ndi makutu athu. Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo. “Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera, kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu. “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.” Kupambana kwa Davide pa Nkhondo Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndi kuwapambana ndipo analanda Metegi Ama kuchoka mʼmanja mwa Afilistiwo. Davide anagonjetsanso Amowabu. Iye anawalamula kuti agone pansi mʼmizere itatu pa gulu lililonse ndipo anawayeza ndi chingwe. Pa gulu lililonse ankapha anthu amene anali pa mizere iwiri yoyamba, kusiyapo mzere wachitatu. Kotero Amowabu anakhala pansi pa ulamuliro wa Davide ndipo ankapereka msonkho. Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. Davide analanda magaleta 1,000, anthu 7,000 okwera magaleta pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha. Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita. Davide anatenga zishango zagolide za akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. Mfumu Davide inatenga mkuwa wambiri kuchokera ku Beta ndi Berotai, mizinda ya Hadadezeri. Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri, anatumiza mwana wake Yoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Yoramu anabweretsa ziwiya zasiliva, zagolide ndi zamkuwa. Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko onse amene anawagonjetsa: Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. Iye anaperekanso zolanda ku nkhondo zochokera kwa Hadadezeri mwana wa Rehobu, mfumu ya Zoba. Ndipo Davide anatchuka atabwera kokakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere. Iye anayika maboma mʼdera lonse la Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita. Akuluakulu a Davide Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika. Zadoki mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Seraya anali mlembi; Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti; ndipo ana a Davide anali ansembe. Davide ndi Mefiboseti Davide anafunsa kuti, “Kodi alipo amene watsala mʼbanja la Sauli kuti ndimuchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?” Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?” Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.” Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?” Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.” Mfumu inafunsa kuti, “Ali kuti?” Ziba anayankha kuti, “Iye ali ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli ku Lodebara.” Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli. Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye. Davide anati, “Mefiboseti!” Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.” Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.” Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?” Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake. Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri). Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu. Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti. Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse. Davide agonjetsa Aamoni Patapita nthawi, mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake Hanuni analowa ufumu mʼmalo mwake. Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake. Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni, atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni mbuye wawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi Davide sanawatumize anthuwa kuti adzaone mzinda wanu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anameta munthu aliyense mbali imodzi ya ndevu zake, ndi kudula zovala zake pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera, ndipo anawabweza kwawo. Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.” Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu. Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene Aaramu a ku Aramu-Zoba ndi Rehobu ndi ankhondo a ku Tobu ndi Maaka anali kwa wokha ku malo wopanda mitengo. Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake, iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.” Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu. Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anasonkhananso. Hadadezeri anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, iwo anapita ku Helamu motsogozedwa ndi Sobaki mkulu wa ankhondo a Hadadezeri. Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye. Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo. Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo. Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni. Davide ndi Batiseba Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu. Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.” Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake. Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?” Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.” Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake. Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.” Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso. Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo. Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi, mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma? Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ” Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene. Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.” Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.” Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro. Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo. Natani Adzudzula Davide Tsono Yehova anatumiza Natani kwa Davide. Atafika kwa Davide anati, “Panali anthu awiri mʼmizinda ina, wina wolemera ndi wina wosauka. Munthu wolemerayo anali ndi nkhosa ndi ngʼombe zambiri, koma wosaukayo analibe chilichonse kupatula kankhosa kamodzi kakakazi kamene anakagula. Iye anakasunga ndipo kanakula naye pamodzi ndi ana ake. Kamadya chakudya chake, kamamwera chikho chake ndipo kamagona mʼmanja mwake. Kanali ngati mwana wamkazi kwa iyeyo. “Ndipo mlendo anafika kwa munthu wolemera uja, koma munthu wolemerayo sanafune kutenga imodzi mwa nkhosa kapena ngʼombe zake kuti akonzere chakudya mlendo amene anafika kwa iye. Mʼmalo mwake anatenga mwana wankhosa wamkazi wa munthu wosauka uja nakonzera chakudya mlendo uja amene anabwera kwa iye.” Davide anapsa mtima kwambiri chifukwa cha munthuyo ndipo anati kwa Natani, “Pali Yehova, munthu amene anachita zimenezi ayenera kufa basi! Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.” Kenaka Natani anati kwa Davide, “Munthuyo ndinu! Yehova, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakudzoza kukhala mfumu ya Israeli, ndipo ndinakupulumutsa mʼdzanja la Sauli. Ndinakupatsanso banja la mbuye wako ndiponso akazi a mbuye wako mʼmanja mwako. Ine ndinakupatsanso banja la Israeli ndi Yuda. Ndipo ngati zinthu zonse izi zinali zochepa, Ine ndikanakupatsa zambiri. Nʼchifukwa chiyani unanyoza mawu a Yehova pochita chimene chili choyipa pamaso pake? Iwe unakantha Uriya Mhiti ndi lupanga ndipo unatenga mkazi wake kukhala wako. Uriyayo unamupha ndi lupanga la Aamoni. Ndipo tsopano lupanga silidzachoka pa nyumba yako, chifukwa unandinyoza ine ndi kutenga mkazi wa Uriya Mhiti kukhala wako.’ “Yehova akuti, ‘Ine ndidzabweretsa tsoka pa iwe lochokera mʼbanja lako. Ndidzatenga akazi ako iwe ukuona ndi kuwapereka kwa wina amene ali pafupi nawe, ndipo iye adzagona ndi akazi ako masanasana Aisraeli onse akuona. Iwe unachita zimenezi mwamseri koma Ine ndidzachita izi masanasana Aisraeli onse akuona.’ ” Kenaka Davide anati kwa Natani, “Ine ndachimwira Yehova.” Natani anayankha kuti, “Yehova wachotsa tchimo lanu. Simufa ayi. Komabe, popeza pochita zimenezi mwachititsa kuti adani a Yehova amunyoze, mwana amene akubalireniyo adzafa.” Natani atapita kwawo, Yehova anakantha mwana amene mkazi wa Uriya anabereka ndipo anayamba kudwala. Davide anapempherera mwanayo kwa Mulungu. Iye anasala chakudya ndipo analowa mʼnyumba mwake nagona pansi usiku wonse. Akuluakulu a banja lake anayima pambali pake kuti amudzutse, koma iye anakana, ndipo sanadye chakudya chilichonse pamodzi ndi iwo. Mwana anamwalira pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Antchito a Davide anaopa kumuwuza kuti mwanayo wamwalira, popeza ankaganiza kuti, “Pamene mwanayu anali ndi moyo, ife tinayankhula Davide koma sanatimvere. Nanga tingamuwuze bwanji kuti mwana wamwalira? Mwina atha kudzipweteka.” Davide anaona kuti antchito ake amanongʼonezana pakati pawo ndipo anazindikira kuti mwanayo wamwalira. Iye anafunsa kuti, “Kodi mwanayo wamwalira?” Iwo anayankha kuti, “Inde wamwalira.” Ndipo Davide anayimirira. Anakasamba nadzola mafuta ndi kusintha zovala zake. Pambuyo pake anapita ku nyumba ya Yehova kukapembedza. Kenaka anapita ku nyumba kwake ndipo atapempha chakudya anamupatsa nadya. Antchito ake anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuchita zinthu motere? Pamene mwana anali ndi moyo, munkasala chakudya ndi kulira, koma tsopano pamene mwana wamwalira inu mukudzuka ndi kudya!” Iye anayankha kuti, “Pamene mwana anali ndi moyo ine ndinkasala zakudya ndi kulira. Ine ndinkaganiza kuti, ‘Akudziwa ndani? Yehova atha kundikomera mtima kuti mwanayo akhale ndi moyo.’ Koma tsopano wamwalira ndisaliranji chakudya? Kodi ndingathe kumubwezanso? Ine ndidzapita kumene kuli iyeko, koma iye sadzabwerera kwa ine.” Ndipo Davide anatonthoza mkazi wake Batiseba, napita kwa iye ndi kugona naye. Iye anabereka mwana wamwamuna, ndipo anamutcha dzina lake Solomoni. Yehova ankamukonda iye. Ndipo chifukwa chakuti Yehova ankamukonda iyeyo, Yehovayo anatumiza mawu kwa mneneri Natani kuti akamutchule Yedidiya. Pa nthawi imeneyi Yowabu anamenyana ndi Raba ku Amoni ndipo analanda nsanja yaufumu. Ndipo Yowabu anatumiza amithenga kwa Davide kukanena kuti, “Ine ndamenyana ndi Raba ndipo ndatenga zitsime zake za madzi. Ndipo tsopano sonkhanitsani asilikali onse ndipo muzungulire mzindawo ndi kuwulanda.” Kotero Davide anasonkhanitsa ankhondo onse ndipo anapita ku Raba kukawuthira nkhondo ndi kuwulanda. Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo ndipo Davide anavala chipewacho. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide, ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa, ndiponso yowomba njerwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka iye pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu. Amnoni ndi Tamara Patapita nthawi, Amnoni mwana wa Davide anakonda Tamara, mlongo wa Abisalomu, mwana wa Davide, amene anali wokongola. Amnoni sankagona tulo mpaka anadwala chifukwa cha Tamara mlongo wakeyo, pakuti iye anali asanagonepo ndi mwamuna ndipo zimaoneka kuti zinali zosatheka kuti achite chilichonse kwa iye. Koma Amnoni anali ndi mnzake dzina lake Yehonadabu mwana wamwamuna wa Simea, mʼbale wake wa Davide. Yonadabu anali munthu wochenjera kwambiri. Iye anafunsa Amnoni, “Nʼchifukwa chiyani iwe mwana wa mfumu, umaoneka wowonda mmawa uliwonse? Bwanji wosandiwuza?” Amnoni anamuyankha kuti, “Ine ndamukonda Tamara, mlongo wa mʼbale wanga Abisalomu.” Yehonadabu anati, “Pita ukagone ndipo unamizire kudwala. Abambo ako akabwera kudzakuona, udzati kwa iwo, Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara abwere kuti adzandikonzere chakudya kuti ndidye. Adzandikonzere chakudyacho ine ndikumuona ndi kudya chili mʼmanja mwake.” Kotero Amnoni anagona nakhala ngati akudwala. Mfumu itabwera kudzamuona, Amnoni anati kwa iyo, “Ine ndikufuna mlongo wanga Tamara kuti abwere adzandipangire buledi wapamwamba ineyo ndikuona, kuti ndidye ali mʼmanja mwake.” Davide anatumiza mawu kwa Tamara ku nyumba yaufumu kuti, “Pita ku nyumba ya mlongo wako Amnoni ndipo ukamukonzere chakudya.” Choncho Tamara anapitadi ku nyumba ya mlongo wake Amnoni kumalo kumene ankagona. Anakanda ufa, nawumba buledi Amunoniyo akuona ndipo anaphika bulediyo. Kenaka iye anatenga chiwaya ndipo anamupatsa bulediyo, koma iyeyo anakana. Amnoni anati “Uza aliyense atuluke muno.” Ndipo aliyense anatuluka. Kenaka Amnoni anati kwa Tamara, “Bweretsa chakudya kuno, ku chipinda changa chogona kuti ndidye chili mʼmanja mwako.” Ndipo Tamara anatenga buledi amene anapanga ndi kubwera naye kwa mlongo wake ku chipinda chake. Koma atabweretsa kwa iye kuti adye, anamugwira ndipo anati, “Bwera ugone nane, iwe mlongo wanga.” Tamara anati kwa iye, “Ayi mlongo wanga! Usandikakamize. Zotere siziyenera kuchitika mu Israeli! Usachite chinthu choyipa chotere. Kodi ukuganiza bwanji za ine? Kodi manyazi anga ndidzawachotsa bwanji? Ndipo nanga iweyo? Udzakhalatu monga mmodzi mwa zitsiru zoyipitsitsa muno mu Israeli. Chonde kapemphe kwa mfumu. Sadzakuletsa kuti undikwatire.” Koma sanamvere zimene amanena Tamara ndipo popeza anali wamphamvu kuposa Tamarayo, iye anamugwirira. Atatero Amnoni anadana naye kwambiri. Iyeyo anamuda kuposa momwe anamukondera. Amnoni anati, “Dzuka ndipo tuluka!” Iye anayankha, “Ayi! Kundithamangitsa kukhala kulakwa kwakukulu kuposa zimene wachita kale kwa ine.” Koma anakana kumumvera. Amnoni anayitana wantchito wake ndipo anati, “Mutulutse mkazi uyu muno ndipo utseke chitseko akatuluka.” Choncho wantchito wakeyo anamutulutsa ndipo anatseka chitseko atatuluka. Tamara anali atavala mkanjo wokongoletsedwa kwambiri, pakuti ichi chinali chovala chimene ana aakazi a mfumu amene sanagonepo ndi mwamuna amavala. Tamara anatsira phulusa pamutu pake ndipo anangʼamba mkanjo wokongoletsedwa umene anavalawo. Iye anagwira manja ake kumutu ndipo anachoka, akulira mokweza pamene amapita. Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa. Mfumu Davide itamva zimenezi, inakwiya kwambiri. Abisalomu sananene mawu aliwonse kwa Amnoni; abwino kapena oyipa. Iye anamuda Amunoniyo chifukwa anachititsa manyazi mlongo wake Tamara. Abisalomu Apha Amnoni Patapita zaka ziwiri, pamene wometa nkhosa za Abisalomu anali ku Baala-Hazori pafupi ndi malire a fuko la Efereimu, iye anayitana ana onse aamuna a mfumu kuti apite kumeneko. Abisalomu anapita kwa mfumu ndipo anati, “Ometa nkhosa za mtumiki wanu anabwera. Chonde mfumu ndi akuluakulu anu mubwere kudzakhala nane?” Mfumu inayankha kuti, “Ayi mwana wanga, tisapite tonsefe. Tidzakhala cholemetsa kwa iwe.” Ngakhale Abisalomu anayesetsa kuwumiriza mfumuyo, inakana kupita. Mʼmalo mwake inangomudalitsa Abisalomuyo. Kenaka Abisalomu anati, “Ngati sizitero, chonde mulole mʼbale wanga Amnoni apite nane.” Mfumu inamufunsa kuti, “Apite nawe chifukwa chiyani?” Koma Abisalomu anamuwumiriza, kotero analola kuti Amnoni pamodzi ndi ana onse a mfumu apite naye. Abisalomu analamula antchito ake kuti, “Tamverani! Amnoni akakaledzera ndi vinyo ndipo ine ndikakanena kuti, ‘Mukantheni Amnoni,’ pamenepo mukamuphe. Musakachite mantha. Kodi ine sindinakulamuleni? Mukhale amphamvu ndipo mulimbe mtima.” Kotero antchito a Abisalomu anachita kwa Amnoni zimene Abisalomu anawalamula. Kenaka ana onse a mfumu anayimirira ndipo anakwera pa abulu awo nathawa. Ali mʼnjira, Davide anamva mphekesera yakuti, “Abisalomu wakantha ana onse a mfumu ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala.” Mfumu inayimirira, ningʼamba zovala zake ndi kugona pa dothi. Antchito ake onse anayimirira pomwepo atangʼamba zovala zawo. Koma Yehonadabu mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anati, “Mbuye wanga mfumu musaganize kuti wapha ana onse a mfumu; wafa ndi Amnoni yekha. Awa ndiwo akhala maganizo a Abisalomu kuyambira tsiku limene Amnoni anagwirira mlongo wake Tamara. Mbuye wanga mfumu musavutike ndi maganizo ndi nkhani yoti ana onse a mfumu afa. Wafa ndi Amnoni yekha.” Nthawi imeneyi nʼkuti Abisalomu atathawa. Tsono munthu amene amalondera anayangʼana ndipo anaona anthu ambiri pa msewu wa kumadzulo kwake, akubwera kutsetsereka phiri. Mlondayo anapita kukawuza mfumu kuti, “Ndikuona anthu pa njira ya Horonaimu, mʼmbali mwa phiri.” Yehonadabu anati kwa mfumu, “Taonani ana a mfumu afika. Zachitika monga momwe mtumiki wanu ananenera.” Pamene amatsiriza kuyankhula, ana a mfumu analowa, akulira mofuwula. Mfumunso ndi antchito ake onse analira mokhudzidwa. Abisalomu anathawa, napita kwa Talimai mwana wa Amihudi, mfumu ya ku Gesuri. Koma mfumu Davide inalira mwana wake tsiku ndi tsiku. Abisalomu atathawa ndi kupita ku Gesuri, anakhala kumeneko zaka zitatu. Ndipo Davide anagwidwa ndi chifundo chofuna kumulondola Abisalomu pakuti anali atatonthozedwa pa imfa ya Amnoni. Abisalomu Abwerera ku Yerusalemu Yowabu mwana wa Zeruya anadziwa kuti maganizo a mfumu ali pa Abisalomu. Kotero Yowabu anatuma munthu wina kupita ku Tekowa ndi kukatengako mkazi wanzeru. Yowabu anati kwa mkaziyo, “Ukhale ngati namfedwa. Uvale zovala zaumasiye ndipo usadzole mafuta ena aliwonse. Ukhale ngati mkazi amene wakhala akulira masiku ambiri. Kenaka upite kwa mfumu ndipo ukayankhule mawu awa.” Ndipo Yowabu anamuwuza mawu oti akanene. Mkazi wochokera ku Tekowa uja atapita kwa mfumu anadzigwetsa pansi, napereka ulemu kwa mfumu nati, “Thandizeni mfumu!” Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi chikukusautsa iwe nʼchiyani?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine mkazi wamasiye, mwamuna wanga anamwalira. Ine wantchito wanu ndinali ndi ana aamuna awiri. Iwo anayamba kumenyana mʼmunda, ndipo panalibe woti awaleretse. Wina anakantha mnzakeyo mpaka kumupha. Tsono banja lonse landiwukira ine, wantchito wanu. Iwo akuti, ‘Utipatse mwana amene anakantha mʼbale wakeyo kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mʼbale wake amene anaphedwayo. Ife tidzaphanso mlowamʼmalo.’ Anthuwo adzapha mwana wanga amene wanditsalira, ndipo dzina la mwamuna wanga silidzakumbukika pakuti sipadzakhalanso mwana pa banja lathu.” Mfumu inati kwa mkaziyo, “Pitani ku nyumba kwanu ndipo ine ndidzalamula mʼmalo mwanu.” Koma mkazi wochokera ku Tekowayo anati kwa mfumu, “Mbuye wanga mfumu, kulakwa kukhale pa ine ndi banja la abambo anga ndipo mfumu ndi mpando wanu waufumu mukhale osalakwa.” Mfumu inayankha kuti, “Ngati wina aliyense anene kanthu kwa iwe, umubweretse kwa ine, ndipo sadzakuvutitsanso.” Mkaziyo anati, “Mfumu ipemphe kwa Yehova Mulungu wake kuti aletse wobwezera imfa asaphenso wina kuti mwana wanga asawonongedwe.” Mfumu inati, “Pali Yehova wamoyo ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pa mwana wako silidzathotholedwa.” Kenaka mkaziyo anati, “Lolani kuti wantchito wanu ayankhule mawu kwa inu mbuye wanga mfumu.” Iye anayankha kuti, “Yankhula.” Mkaziyo anati, “Nʼchiyani tsono chimene mwaganiza kuchitira zimenezi anthu a Mulungu? Pamene mfumu yanena izi, kodi sikudzitsutsa yokha, pakuti mfumu sinayitanitse mwana amene anamupirikitsa? Koma poti madzi akatayika sawoleka, ndiye tonsefe tiyenera kufa ndithu. Koma Mulungu safuna kuti moyo wa munthu utayike kotero anakonza njira yakuti wopirikitsidwayo asakhale wotayikiratu. “Tsopano ine ndabwera kudzanena izi kwa inu mbuye wanga mfumu chifukwa anthu andichititsa mantha. Mdzakazi wanu anaganiza kuti, ‘Ndikayankhula kwa mfumu, mwina adzachita zimene mdzakazi wake adzamupempha. Mwina mfumu idzavomereza kupulumutsa mdzakazi wake mʼdzanja la munthu amene akufuna kupha ine pamodzi ndi mwana wanga kutichotsa pa cholowa chimene Mulungu anatipatsa.’ “Ndipo tsopano mtumiki wanu akuti, ‘Lolani mawu a mbuye wanga mfumu abweretse mpumulo kwa ine, pakuti mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu pozindikira chabwino ndi choyipa. Yehova Mulungu wanu akhale nanu.’ ” Kenaka mfumu inati kwa mkaziyo, “Usandibisire chilichonse pondiyankha chimene ndidzakufunsa.” Mkaziyo anati, “Mbuye wanga mfumu yankhulani.” Mfumu inafunsa kuti, “Kodi zimenezi sukuchita motsogozedwa ndi Yowabu?” Mkaziyo anayankha kuti, “Pali inu wamoyo, mbuye wanga mfumu, palibe munthu angakhotere kumanja kapena kumanzere pa chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mwanena. Inde, ndi mtumiki wanu Yowabu amene wandilangiza ine kuchita zimenezi ndipo ndi amene anandipatsa mawu onsewa woti ine mtumiki wanu ndiyankhule. Mtumiki wanu Yowabu anachita zimenezi kuti asinthe mmene zinthu zilili lero. Mbuye wanga muli ndi nzeru ngati za mngelo wa Mulungu. Mumadziwa zonse zimene zikuchitika mʼdziko.” Mfumu inati kwa Yowabu, “Chabwino, ine ndichita zimenezi. Pita kamutenge Abisalomuyo.” Yowabu anawerama pansi kupereka ulemu kwa mfumu. Yowabuyo anati, “Lero mtumiki wanu wadziwa kuti wapeza chifundo pamaso panu, mbuye wanga mfumu, chifukwa mwavomera pempho lakeli.” Choncho Yowabu anapita ku Gesuri ndipo anamubweretsa Abisalomu ku Yerusalemu. Koma mfumu inati, “Iye apite ku nyumba yake; asaone nkhope yanga.” Kotero Abisalomu anapita ku nyumba yake ndipo sanakumane ndi mfumu. Mʼdziko lonse la Israeli munalibe munthu amene anayamikidwa chifukwa cha maonekedwe ake wokongola ngati Abisalomu. Kuyambira kumutu mpaka ku mapazi ake, analibe chilema. Nthawi ina iliyonse akamameta tsitsi lake, ankameta pamene layamba kumulemera. Akatero amaliyeza, ndipo limalemera makilogalamu awiri pa sikelo yaufumu. Abisalomu anali ndi ana aamuna atatu ndi wamkazi mmodzi. Mwana wamkazi dzina lake linali Tamara, ndipo anali mkazi wokongola kwambiri. Abisalomu anakhala zaka ziwiri mu Yerusalemu osaonekera kwa mfumu. Kenaka Abisalomu anatumiza mawu kwa Yowabu, kumutuma kuti apite kwa mfumu, koma Yowabu anakana kubwera. Kotero anatumizanso mawu kachiwiri, koma Yowabu anakananso. Tsono Abisalomu anati kwa antchito ake, “Taonani, munda wa Yowabu uli pafupi ndi wanga ndipo muli barele mʼmenemo. Pitani mukawutenthe mundawo.” Ndipo antchito a Abisalomu anawutentha mundawo. Ndipo Yowabu anapita ku nyumba ya Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani antchito ako atentha munda wanga?” Abisalomu anati kwa Yowabu, “Taona, ine ndinatumiza mawu kwa iwe ndipo ndinati, ‘Bwera kuno kuti ndikutume kwa mfumu kukafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ine ndinabwera kuchokera ku Gesuri? Zikanakhala bwino ndikanakhala komweko!’ Tsono pano ndikufuna kuonana ndi mfumu, ndipo ngati ndili olakwa mfumuyo indiphe.’ ” Choncho Yowabu anapita kwa mfumu ndipo anayiwuza zimenezi. Ndipo mfumu inamuyitanitsa Abisalomu, ndipo analowa nawerama kugunditsa nkhope yake pansi pamaso pa mfumu. Tsono mfumu inapsompsona Abisalomu. Abisalomu Akonzekera Zowukira Patapita nthawi, Abisalomu anadzipezera galeta ndi akavalo pamodzi ndi amuna makumi asanu amene amathamanga patsogolo pake. Iye amadzuka mmamawa ndi kuyima pa njira yopita ku chipata cha mzinda. Munthu wina aliyense akakhala ndi zodandaula zopita nazo kwa mfumu kuti akaweruze, Abisalomu amamuyitana iye ndi kumufunsa kuti, “Kodi ukuchokera ku limodzi mwa mafuko a Israeli?” Kenaka Abisalomu amanena kwa iye kuti, “Taona, madandawulo ako ndi abwino ndi oyenera, koma palibe woyimira mfumu woti akumvere.” Ndipo Abisalomu amawonjezera kunena kuti, “Ine ndikanangosankhidwa kukhala woweruza mʼdziko muno bwenzi munthu aliyense amene ali ndi madandawulo kapena milandu akubwera kwa ine ndipo ndikanaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.” Ndipo nthawi zonse amati munthu akasendera pafupi ndi kumugwandira, Abisalomu amatambalitsa dzanja lake, kumuyimiritsa munthuyo ndi kupsompsona. Abisalomu amachitira izi Aisraeli onse amene amabwera kwa mfumu kuti adzaweruzidwe ndipo Abisalomuyo anagwira mtima anthu a mu Israeli. Patapita zaka zinayi Abisalomu anati kwa mfumu, “Loleni ndipite ku Hebroni kuti ndikakwaniritse lonjezo limene ndinachita kwa Yehova. Pamene mtumiki wanu amakhala ku Gesuri ku Aramu, anachita lonjezo ili: ‘Ngati Yehova adzandibweretsadi ku Yerusalemu, ndidzapembedza Yehovayo mu Hebroni.’ ” Mfumu inati kwa iye, “Pita mu mtendere” Kotero iye anapita ku Hebroni. Ndipo Abisalomu anatuma amithenga ake mwamseri kwa mafuko onse a Israeli kukanena kuti, “Mukangomva kulira kwa malipenga pamenepo munene kuti, ‘Abisalomu ndiye mfumu mu Hebroni.’ ” Anthu 200 ochokera mu Yerusalemu anapita naye Abisalomu. Iwo anayitanidwa monga alendo ndipo anapita osadziwa chilichonse pa nkhaniyi. Pamene Abisalomu amapereka nsembe, iye anayitanitsanso Ahitofele Mgiloni, mlangizi wa Davide, wa ku Gilo, kotero kuwukiraku kunakula kwambiri, ndipo anthu otsatira Abisalomu anapitirira kuchuluka. Davide Athawa Abisalomu Munthu wina anabweretsa uthenga ndi kudzamuwuza Davide kuti, “Mitima ya Aisraeli onse ili pa Abisalomu.” Ndipo Davide anati kwa akuluakulu ake amene anali mu Yerusalemu. “Bwerani! Tiyeni tithawe, mwina palibe adzapulumuke kwa Abisalomu. Tiyeni tichoke msanga, mwina iye adzabwera msanga ndi kutipitirira, nʼkuwononga ife ndi mzinda wathu ndi lupanga.” Akuluakulu a mfumu anamuyankha kuti, “Antchito anu ndi okonzeka kuchita chilichonse chimene mbuye wathu mfumu mukufuna kuchita.” Mfumu inanyamuka pamodzi ndi banja lake lonse. Koma iye anasiya azikazi khumi kuti azisamalira nyumba yaufumu. Kotero mfumu inanyamuka pamodzi ndi anthu onse oyitsatira, ndipo anayima pamalo pena chapatalipo. Ankhondo ake onse anayamba kuyenda pamaso pa Davide, ndipo Akereti ndi Apeleti, pamodzinso ndi Agiti okwanira 600 amene anamutsata kuchokera ku Gati, nawonso anayenda pamaso pake. Mfumu inati kwa Itai Mgiti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ukupita ndi ife? Bwerera ndipo ukakhale ndi mfumu Abisalomu. Iwe ndiwe mlendo munthu wothawa kwawo. Wangobwera dzulo lomweli, lero ndikutenge kuti uziyendayenda ndi ife, pamene ine sindikudziwa kumene ndikupita? Bwerera, ndipo tenga abale ako. Chifundo ndi kukhulupirika zikhale nawe.” Koma Itai anayankha mfumu kuti, “Pali Yehova wamoyo, kulikonse kumene mbuye wanga mfumu mudzakhala, kaya ndi moyo kapena imfa, mtumiki wanu adzakhala komweko.” Davide anati kwa Itai, “Tiye pita nafe” Kotero Itai Mgiti anayenda pamodzi ndi anthu ake ndi mabanja amene anali naye. Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu. Zadoki anali nawonso, ndipo Alevi onse amene anali naye ananyamula Bokosi la Chipangano la Mulungu. Iwo anayika pansi Bokosi la Mulungulo ndipo Abiatara ankapereka nsembe mpaka pamene anthu onse anamaliza kutuluka mu mzinda. Kenaka mfumu inati kwa Zadoki, “Tenga Bokosi la Mulungu ubwerere nalo mu mzinda. Ngati ndidzapeza chifundo pamaso pa Yehova, adzandibweretsa kuti ndilionenso ndi malo ake okhalamo. Koma iye anati, ‘Akapanda kukondwera nane,’ chabwino, andichite chimene chimukomere.” Mfumu inatinso kwa wansembe Zadoki, “Kodi siwe mlosi? Bwerera mu mzinda mwamtendere pamodzi ndi mwana wako Ahimaazi ndi Yonatani mwana wa Abiatara. Iwe ndi Abiatara tengani ana anu awiri. Ine ndidzadikira powolokera Yorodani ku chipululu mpaka nditalandira mawu ochokera kwa iwe ondiwuza mmene zilili zinthu.” Kotero Zadoki ndi Abiatara ananyamula Bokosi la Mulungu lija nabwerera nalo ku Yerusalemu, ndipo anakakhala kumeneko. Koma Davide anapitirira ndi kukakwera phiri la Olivi akupita nalira. Anafunda kumutu koma sanavale nsapato. Anthu onse amene anali naye anafundanso kumutu, ndipo nawonso amalira pamene amapita. Tsono Davide anamva kuti, “Ahitofele ali pakati pa anthu owukira pamodzi ndi Abisalomu.” Choncho Davide anapemphera, “Inu Yehova, musandutse uphungu wa Ahitofele ukhale uchitsiru.” Davide atafika pamwamba pa phiri pomwe anthu ankapembedzerapo Mulungu, Husai Mwariki anadzakumana naye atangʼamba mkanjo wake ndi kudzithira fumbi kumutu. Davide anati kwa iye, “Ngati iwe upite ndi ine, udzakhala chondilemetsa. Koma ngati ubwerera ku mzinda ndi kukanena kwa Abisalomu kuti, ‘Inu mfumu ine ndidzakhala wantchito wanu.’ Mʼmbuyomu ndinali wantchito wa abambo anu koma tsopano ndidzakhala wantchito wanu. Ukatero udzandithandiza kulepheretsa malangizo a Ahitofele. Kodi ansembe, Zadoki ndi Abiatara, sakukhala nawe kumeneko? Ukawawuze zonse zimene umamva mʼnyumba yaufumu. Ana awo awiri, Ahimaazi wa Zadoki, ndi Yonatani mwana wa Abiatara ali nawo pamodzi, uzikawatuma kwa ine ndi china chilichonse chimene ukamve.” Ndipo Husai bwenzi la Davide anafika ku Yerusalemu pamene Abisalomu amalowa mu mzinda. Davide ndi Ziba Davide atapitirira pangʼono pamwamba pa phiri, anakumana ndi Ziba mtumiki wa Mefiboseti akudikira kuti akumane naye. Iye anali ndi abulu a chishalo pa msana ndipo ananyamula malofu a buledi 200, ntchintchi 100 za mphesa zowuma, zipatso za pa nthawi yachilimwe 100 ndi thumba la vinyo. Mfumu inafunsa Ziba kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabweretsa izi?” Ziba anayankha kuti, “Abuluwa ndi oti anthu a mʼbanja mwanu akwerepo, buledi ndi zipatso ndi za anthu anu kuti adye, ndipo vinyoyo ndi woti atsitsimutse anthu amene atope mʼchipululu.” Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?” Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ” Ndipo mfumu inati kwa Ziba, “Zonse zimene zinali za Mefiboseti ndi zako tsopano.” Ziba anati, “Ine modzichepetsa ndikukugwandirani, mbuye wanga mfumu, kuti ndipeze chisomo pamaso panu.” Simei Atukwana Davide Mfumu Davide itayandikira Bahurimu, munthu wochokera ku fuko limodzi ndi banja la Sauli anabwera kuchokera mʼmenemo. Dzina lake linali Simei, mwana wa Gera ndipo amatukwana pamene amabwera. Iye amagenda Davide miyala ndi akuluakulu onse a mfumu, ngakhale kuti ankhondo onse ndi oteteza Davide anali ali kumanzere ndi kumanja kwake. Potukwana, Simeiyo amati, “Choka iwe, choka iwe, munthu wopha anthu, munthu wachabechabe iwe! Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!” Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.” Koma mfumu inati, “Inu ana a Zeruya, kodi ndikuchitireni chiyani? Ngati iye akutukwana chifukwa Yehova wamuwuza kuti, ‘Tukwana Davide,’ angafunse ndani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?’ ” Tsono Davide anati kwa Abisai ndi akuluakulu ake onse, “Mwana wanga wobereka ndekha akufuna kundipha. Nanji tsono munthu wa fuko la Benjamini uyu! Musiyeni; mulekeni atukwane pakuti Yehova wachita kumuwuza kuti atero. Mwina Yehova adzaona mazunzo anga ndipo adzandibwezera zabwino chifukwa cha kutukwanidwa kumene ndikulandira lero.” Kotero Davide ndi anthu ake anapitirira kuyenda mu msewu pamene Simei amayenda mʼmbali mwa phiri moyangʼanana naye akutukwana ndi kuponya miyala pamene amayenda nʼkumamutsiranso dothi. Mfumu ndi anthu ake onse anafika kumene amapita atatopa kwambiri. Ndipo kumeneko anapumula. Malangizo a Husai ndi Ahitofele Pa nthawi imeneyi Abisalomu ndi Aisraeli ena onse anabwera ku Yerusalemu, Ahitofele anali naye. Tsono Husai Mwariki bwenzi la Davide anapita kwa Abisalomu ndipo anati kwa iye, “Ikhale ndi moyo wautali mfumu! Ikhale ndi moyo wautali mfumu!” Abisalomu anafunsa Husai, “Kodi ichi ndi chikondi chimene ukumuonetsa bwenzi lako? Nʼchifukwa chiyani sunapite ndi bwenzi lako?” Husai anati kwa Abisalomu, “Ayi, ndidzakhala wake wa amene Yehova wamusankha, wosankhidwa ndi anthu awa ndi anthu onse a Israeli, ndipo ndidzakhala wake nthawi zonse. Kodi ndidzatumikiranso yani? Kodi sinditumikira mwana wa mfumu? Monga momwe ndinatumikira abambo anu, kotero ndidzatumikiranso inu.” Abisalomu anati kwa Ahitofele, “Tiwuze malangizo ako. Kodi tichite chiyani?” Ahitofele anayankha kuti, “Mugone ndi azikazi a abambo anu amene awasiya kuti asamalire nyumba yaufumu. Aisraeli onse adzamva kuti mwachitira abambo anu chinthu chonyansa kotheratu ndipo anthu onse amene ali ndi iwe adzalimbikitsidwa.” Choncho anamangira tenti Abisalomu pa denga la nyumba ndipo iye anagona ndi azikazi a abambo ake Aisraeli onse akuona. Tsono masiku amenewo malangizo amene Ahitofele amapereka anali ngati mawu ochokera kwa Mulungu. Umu ndi mmene Davide ndi Abisalomu amalandirira malangizo onse a Ahitofele. Ahitofele anati kwa Abisalomu, “Mundilole ndisankhe asilikali 12,000, ndinyamuke usiku womwe uno kuti ndithamangire Davide. Ndipo ndikamuthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima. Ndikamuchititsa mantha ndipo anthu onse amene ali naye akathawa. Ine ndikakantha mfumu yokhayo, ndipo anthu onse ndidzabwera nawo kwa inu, ngati mkwati amene akubwerera kwa mwamuna wake. Imfa ya munthu mmodzi yekha idzakhalitsa anthu onse pa mtendere.” Malangizo awa anaoneka abwino kwa Abisalomu ndi kwa akuluakulu onse a Israeli. Koma Abisalomu anati, “Muyitanenso Husai Mwariki kuti timve zimene iye adzanena.” Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.” Husai anayankha Abisalomu kuti, “Malangizo amene Ahitofele wapereka si abwino pa nthawi ino. Inu mukudziwa bwino abambo anu ali ndi ankhondo awo. Iwo ndi anthu ankhondo komanso ndi woopsa ngati chimbalangondo chimene chalandidwa ana ake. Kuwonjezera apa abambo anu ndi katswiri wa nkhondo. Iwo sanagone pamodzi ndi asilikali awo. Onani, ngakhale tsopano lino abisala mʼphanga lina ku malo ena ake. Ngati iwo atayamba kuthira nkhondo asilikali anu, aliyense amene adzamve zimenezi adzati, ‘Gulu lalikulu lankhondo lotsatira Abisalomu laphedwa.’ Tsono ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiri, amene mtima wake uli ngati wa mkango, adzagwidwa ndi mantha aakulu pakuti Aisraeli akudziwa kuti abambo anu ndi ankhondo ndipo kuti iwo amene ali nawo ndi anthu olimba mtima. “Kotero ine ndikukulangizani kuti: Aisraeli onse, kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba; ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja, asonkhane kwa inu ndipo muwatsogolera kupita ku nkhondo. Ndipo ife tidzapita kukamuthira nkhondo kulikonse kumene tikamupeze, ndipo ife tikamuthira nkhondo ngati mame pa nthaka. Palibe amene adzakhale wamoyo kaya iye kapena ankhondo ake. Iye akakathawira mu mzinda, Aisraeli onse adzabweretsa zingwe ku mzindawo, ndipo ife tidzawugwetsera ku chigwa mpaka sipadzapezeka ngakhale kachidutswa.” Abisalomu ndi ankhondo ena onse a Israeli anati, “Malangizo a Husai Mwariki ndi abwino kuposa a Ahitofele.” Pakuti Yehova anatsimikiza kutsutsa malangizo onse abwino a Ahitofele ndi cholinga choti zimuvute Abisalomu. Husai anawuza ansembe Zadoki ndi Abiatara kuti, “Ahitofele analangiza Abisalomu ndi akuluakulu a Israeli zakuti, koma ine ndawalangiza kuchita zakutizakuti. Tsopano tumizani wamthenga msangamsanga kuti akamuwuze Davide kuti, ‘Musakagone powolokera Yorodani ku chipululu koma mukawoloke. Mukapanda kutero, mfumu ndi anthu onse amene ali naye adzaphedwa.’ ” Yonatani ndi Ahimaazi amakhala ku Eni Rogeli. Tsono wantchito wamkazi ndiye amapita kukawawuza ndipo iwo amayenera kupita kukamuwuza mfumu Davide, pakuti iwowo sankayenera kuonekera polowa mu mzinda. Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo. Mkazi wake anatenga chophimba ndipo anachiyika pamwamba pa chitsimecho nawazapo tirigu. Palibe amene anadziwa chilichonse za izi. Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?” Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu. Anthu aja atapita, awiriwo anatuluka mʼchitsimemo ndipo anapita kukawuza mfumu Davide nati kwa iye, “Nyamukani, muwoloke mtsinje msangamsanga. Ahitofele wapereka malangizo akutiakuti kutsutsana nanu.” Kotero Davide ndi anthu onse amene anali nawo ananyamuka ndi kuwoloka Yorodani. Pofika mmamawa, panalibe munthu amene anatsala asanawoloke Yorodani! Ahitofele ataona kuti malangizo ake sanatsatidwe, iye anakwera bulu wake napita ku mzinda wa kwawo ku nyumba yake. Iye anakonza mʼnyumba mwakemo ndi kudzimangirira. Kotero anafa nayikidwa mʼmanda a abambo ake. Davide anapita ku Mahanaimu, ndipo Abisalomu anawoloka Yorodani pamodzi ndi ankhondo ena onse a Israeli. Abisalomu anasankha Amasa kukhala mkulu wa ankhondo mʼmalo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wotchedwa Itira Mwisraeli amene anakwatira Abigayeli mwana wa Nahasi mlongo wake wa Zeruya, amayi ake a Yowabu. Aisraeli ndi Abisalomu anamanga zithando mʼdziko la Giliyadi. Davide atafika ku Mahanaimu, Sobi mwana wa Nahasi wochokera ku Raba ku dziko la Amoni ndi Makiri mwana wa Amieli wochokera ku Lodebara, ndi Barizilai Mgiliyadi wochokera ku Rogelimu anabweretsa zofunda, mabeseni ndi miphika. Iwo anabweretsanso kwa Davide ndi anthu ake zakudya izi: tirigu ndi barele, ufa ndi tirigu wokazinga, nyemba ndi mphodza, uchi ndi chambiko, nkhosa ndi mafuta olimba a mkaka wangʼombe. Pakuti anati, “Anthuwa ali ndi njala ndipo atopa, alinso ndi ludzu muno mʼchipululu.” Imfa ya Abisalomu Davide anasonkhanitsa anthu amene anali naye ndipo anasankha atsogoleri ena olamulira ankhondo 1,000 ndi ena olamulira ankhondo 100. Davide anatumiza asilikaliwo atawagawa patatu: gulu loyamba limalamulidwa ndi Yowabu, gulu lachiwiri limalamulidwa ndi Abisai ndipo gulu lachitatu limalamulidwa ndi Itai Mgiti. Mfumu inawuza asilikaliwo kuti, “Inenso ndipita nanu ndithu.” Koma anthuwo anati, “Inu musapite nafe. Ngati tidzathamangitsidwa, iwowo sadzasamala za ife. Ngakhale theka la ife litafa, iwo sadzasamalako. Koma inuyo ndinu ofunika kuposa asilikali 10,000. Nʼkwabwino kwambiri kuti inu muzititumizira chithandizo kuchokera ku mzindako.” Mfumu inayankha kuti, “Ine ndichita chimene chili chokukomerani.” Kotero mfumu inayima pambali pa chipata pamene ankhondo onse amayenda mʼmagulu a anthu 100 ndi a 1,000. Mfumu inalamulira Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumukomere mtima Abisalomu chifukwa cha ine.” Ndipo asilikali onse anamva pamene mfumu imalamula izi za Abisalomu kwa wolamulira aliyense. Ankhondo anayenda kupita kukachita nkhondo ndi Israeli, ndipo nkhondo inachitika mʼnkhalango ya Efereimu. Aisraeli anagonjetsedwa kumeneko ndi ankhondo a Davide. Tsiku limenelo anaphedwa anthu okwanira 20,000. Nkhondo inafalikira ku madera onse akumidzi ndipo anthu akufa chifukwa cha zoopsa za mʼnkhalango anali ambiri tsiku limenelo kuposa akufa ndi lupanga. Tsono zinachitika kuti Abisalomu anakumana ndi asilikali a Davide. Iye anali atakwera bulu ndipo pamene buluyo amadutsa pansi pa nthambi zambiri za mtengo wa thundu, mutu wa Abisalomu unakodwa mu mtengomo. Iye anasiyidwa atatsakamira mʼmalele, pamene bulu amene anakwerapoyo amapitirira. Mmodzi mwa asilikali ataona zimenezi, anamuwuza Yowabu kuti, “Ine ndamuona Abisalomu ali lende mu mtengo wa thundu.” Yowabu anati kwa munthu amene anamuwuza zimenezi, “Ukuti chiyani! Unamuona? Nʼchifukwa chiyani sunamukanthire pansi pomwepo? Ndipo ine ndikanakupatsa ndalama za siliva khumi ndi lamba wausilikali.” Koma munthuyo anayankha kuti, “Ngakhale atandipatsa mʼmanja mwanga ndalama zasiliva 1,000, sindingatambasule dzanja langa kupha mwana wa mfumu. Ife tikumva, mfumu inalamula inu Abisai ndiponso Itai kuti, ‘Mutetezeni mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ine!’ Ndipo sindikanayika moyo wanga pa chiswe pakuti palibe chimene chimabisika pamaso pa mfumu komanso inu simukanditeteza.” Yowabu anati, “Ine sinditayanso nthawi ndi iwe.” Ndipo anatenga mikondo itatu mʼmanja mwake ndipo anabaya pamtima pa Abisalomu, Abisalomuyo akanali ndi moyo pa mtengo wa thundu. Ndipo anthu khumi onyamula zida za Yowabu anazungulira Abisalomu, kumubaya ndi kumupha. Kenaka Yowabu analiza lipenga ndipo asilikali analeka kuthamangitsa Israeli pakuti Yowabu anawaletsa. Iwo anatenga Abisalomu ndi kumuponya mʼdzenje lalikulu mʼchipululumo ndipo anawunjikapo miyala ikuluikulu. Nthawiyi Aisraeli onse anathawa kupita ku nyumba zawo. Abisalomu ali ndi moyo anadzimangira chipilala mʼchigwa cha mfumu, pakuti ankaganiza kuti, “Ine ndilibe mwana wamwamuna amene adzakhale chikumbutso changa.” Chipilalacho anachitchula dzina lake lomwe ndipo mpaka lero chimatchedwa chipilala cha Abisalomu. Davide Alira Abisalomu Tsono Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, “Ndiloleni ndithamange ndi kukapereka uthenga kwa mfumu kuti Yehova wayipulumutsa mʼdzanja la adani ake.” Yowabu anamuwuza iye kuti, “Iwe si amene uti ukanene zimenezi lero. Ukapereka uthenga nthawi ina, koma usatero lero, chifukwa mwana wa mfumu wafa.” Kenaka Yowabu anawuza Mkusi kuti, “Pita ukawuze mfumu zimene waona.” Mkusiyo anawerama pamaso pa Yowabu ndipo anathamanga kupita. Ahimaazi mwana wa Zadoki ananenanso kwa Yowabu kuti, “Zivute zitani, chonde mundilole kuti ndipite pambuyo pa Mkusiyo.” Koma Yowabu anayankha kuti, “Mwana wanga, nʼchifukwa chiyani ukufuna kupita? Ulibe nkhani yoti ukalandire nayo mphotho.” Iye anati, “Zivute zitani ine ndikufuna kuti ndipite.” Choncho Yowabu anati “Pita!” Ndipo Ahimaazi anathamanga kudzera njira ya ku chigwa ndipo anamupitirira Mkusi uja. Nthawi imeneyo nʼkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziwiri, chakubwalo ndi chamʼkati. Mlonda anakwera pa khoma nakayimirira pa denga la chipata. Anati atayangʼana, anaona munthu akuthamanga yekhayekha. Mlonda uja anapita kwa mfumu ndipo anafotokoza. Mfumu inati, “Ngati ali yekha ali ndi nkhani yabwino” Ndipo munthuyo anayandikira. Mlonda uja anaonanso munthu wina akuthamanga, ndipo anayitana woyangʼanira pa chipata, “Taona, munthu winanso akuthamanga ali yekha!” Mfumu inati, “Iye akubweretsanso nkhani yabwino.” Mlonda uja anati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi mmene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu inati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.” Ndipo Ahimaazi anafuwula kwa mfumu, “Zonse zili bwino!” Iye anagwada pamaso pa mfumu nkhope yake atagunditsa pansi ndipo anati, “Yehova Mulungu wathu alemekezedwe! Iye wapereka mʼdzanja lathu anthu amene anawukira inu mbuye wanga mfumu.” Mfumu inafunsa, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?” Ahimaazi anayankha, “Pamene Yowabu amati azindituma ine mtumiki wanu ndinaona chipiringu cha anthu, koma sindikudziwa chinali chiyani.” Mfumu inati, “Ima apo ndipo udikire.” Kotero iye anapita pa mbali nayima pamenepo. Kenaka Mkusi uja anafika ndipo anati, “Mbuye wanga mfumu imvani nkhani yabwino! Yehova wakupulumutsani inu lero kwa onse amene anakuwukirani.” Mfumu inafunsa Mkusiyo kuti, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?” Mkusiyo anayankha kuti, “Adani anu mbuye wanga mfumu, pamodzi ndi anthu onse amene amakuwukirani, ziwaonekere zomwe zamuonekera mnyamatayo.” Mfumu inanthunthumira. Inapita ku chipinda cha mmwamba cha pa chipata kukalira. Pamene imapita, inkati: “Iwe mwana wanga Abisalomu! Mwana wanga! Mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine mʼmalo mwako! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” Yowabu anawuzidwa kuti, “Mfumu ikulira maliro a Abisalomu.” Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake. Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo. Mfumu inaphimba nkhope yake ndipo inalira mofuwula, “Iwe mwana wanga Abisalomu! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!” Kenaka Yowabu analowa mʼnyumba ya mfumu nafika kwa mfumuyo ndipo anati, “Lero mwachititsa manyazi asilikali anu onse, amene apulumutsa moyo wanu ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu. Inu mumakonda amene amadana nanu ndipo mumadana ndi amene amakukondani. Inuyo mwaonetsa lero poyera kuti simusamala za atsogoleri anu a nkhondo ndi asilikali awo. Ine ndikuona kuti inu mukanakondwera ngati Abisalomu akanakhala ndi moyo lero, tonsefe titafa. Tsopano pitani mukawalimbikitse asilikali anu. Ine ndikulumbira mwa Yehova kuti ngati inu simupita palibe munthu amene adzatsale ali ndi inu polowa dzuwa. Ichi chidzakhala choyipa kwambiri kuposa zovuta zonse zimene zinakugwerani kuyambira muli mnyamata mpaka lero.” Kotero mfumu inanyamuka ndipo inakhala pa mpando wake pa chipata. Pamene asilikali anawuzidwa kuti, “Mfumu yakhala pa chipata,” onse anabwera kwa iye. Davide Abwerera ku Yerusalemu Nthawi imeneyi nʼkuti Aisraeli atathawira ku nyumba zawo. Pakati pa mafuko onse a Israeli, anthu amakangana ndipo amati, “Mfumu inatipulumutsa mʼmanja mwa adani anthu. Iye ndi amene anatilanditsa mʼdzanja la Afilisti. Koma tsopano wathawa mʼdziko muno chifukwa cha Abisalomu. Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?” Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo. Inu ndinu abale anga enieni, mafupa anga ndi mnofu wanga. Nʼchifukwa chiyani inuyo mukukhala otsiriza kubweretsa mfumu?’ Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’ ” Davide anakopa mitima ya anthu onse a Yuda ndipo anthuwo anakhala ngati munthu mmodzi. Iwo anatumiza mawu kwa mfumu, “Bwererani inu ndi anthu anu onse.” Kotero mfumu inabwerera ndipo inakafika mpaka ku Yorodani. Tsono anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala kuti akakumane ndi mfumu ndi kumuwolotsa Yorodani. Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide. Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu. Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna. Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga musaganizire za kulakwa kwanga. Musakumbukire zolakwa zimene mtumiki wanu anakuchitirani tsiku limene mbuye wanga mfumu mumachoka mu Yerusalemu. Mfumu musazikumbukirenso zimenezi. Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.” Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati, “Kodi Simei saphedwa chifukwa cha ichi? Iye anatukwana wodzozedwa wa Yehova.” Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?” Ndipo mfumu inati kwa Simei, “Iwe Simei suphedwa.” Ndipo mfumuyo inalonjeza ndi lumbiro. Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake. Pamene anafika kuchokera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?” Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa. Ndipo wayankhula zosinjirira za ine mtumiki wanu kwa inu mbuye wanga mfumu. Mbuye wanga mfumu ali ngati mngelo wa Mulungu ndipo chitani chimene chikukomerani. Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?” Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.” Mefiboseti anati kwa mfumu, “Muloleni atenge zonse, pakuti tsopano mbuye wanga mwafika kwanu mu mtendere.” Barizilai Mgiliyadi anabweranso kuchokera ku Rogelimu kudzawoloka Yorodani ndi mfumu ndi kumuperekeza kuchokera kumeneko. Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri. Mfumu inati kwa Barizilai, “Woloka nane ndipo ukakhale ndi ine mu Yerusalemu ndipo ineyo ndidzakusamalira.” Barizilai anayankha mfumu kuti, “Kodi zakhala zaka zingati zoti ndikhale ndi moyo, kuti ndipite ku Yerusalemu ndi mfumu? Ine tsopano ndili ndi zaka 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa? Kodi mtumiki wanu angathe kuzindikira kukoma kwa zimene akudya ndi kumwa? Kodi ndingathe kumva kuyimba kwa amuna ndi akazi? Nʼchifukwa chiyani wantchito wanu akakhale ngati katundu kwa mbuye wanga mfumu? Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pangʼono kuti ndiwoloke Yorodani pamodzi ndi mfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere? Muloleni, mtumiki wanu abwerere, kuti ndikafere kwathu pafupi ndi manda a abambo ndi amayi anga. Koma nayu mtumiki wanu Kimuhamu. Muloleni iye awoloke nanu mbuye wanga mfumu. Mumuchitire chilichonse chimene chikukomereni!” Mfumu inati, “Kimuhamu adzawoloka ndi ine, ndipo ndidzamuchitira iye chilichonse chimene chidzakondweretsa iwe. Ndipo chilichonse chimene udzandipempha ine ndidzakuchitira.” Kotero anthu onse anawoloka Yorodani ndipo kenaka mfumu inawoloka. Mfumu inapsompsona Barizilai ndi kumupatsa madalitso ndipo Barizilaiyo anabwerera kwawo. Pamene mfumu inawolokera ku Giligala, Kimuhamu anawoloka naye. Ankhondo onse a Yuda ndi theka la ankhondo a Israeli onse anaperekeza mfumu. Kenaka Aisraeli onse amabwera kwa mfumu nʼkumati kwa iye, “Nʼchifukwa chiyani abale athu, anthu a ku Ayuda, anakubani mfumu, nawoloka nanu Yorodani inu ndi banja lanu, pamodzi ndi anthu ake onse?” Ayuda onse anayankha Aisraeli kuti, “Ife timachita zimenezi chifukwa mfumu ndi mʼbale wathu. Nʼchifukwa chiyani inu mwapsa mtima ndi zimenezi? Kodi ife tinadya chakudya chilichonse cha mfumu? Kodi chilipo chimene ife tatenga kukhala chathu?” Aisraeli anayankha Ayuda kuti, “Ife ndi magawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo kuwonjezera apo, ife tili ndi zinthu zambiri mwa Davide kuposa inu. Tsono nʼchifukwa chiyani mukutichita chipongwe? Kodi ife si amene tinayamba kunena za kubweretsa mfumu yathu?” Koma anthu a Yuda anayankha mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israeli. Seba Awukira Davide Ndipo munthu wina wokonda kuyambitsa chisokonezo, dzina lake Seba, mwana wa Bikiri wa fuko la Benjamini, anali komweko. Iye analiza lipenga ndipo anafuwula kuti, “Ife tilibe chathu mu mfumu wa Davide, tilibe gawo mwa mwana wa Yese! Inu Aisraeli aliyense apite ku nyumba kwake!” Kotero Aisraeli onse anamuthawa Davide ndipo anatsatira Seba mwana wa Bikiri. Koma anthu a ku Yuda anakhala ndi mfumu yawo njira yonse kuchokera ku Yorodani mpaka ku Yerusalemu. Davide atabwerera ku nyumba yake yaufumu ku Yerusalemu, iye anatenga azikazi khumi aja amene anawasiya kuti aziyangʼanira nyumba yaufumu, ndipo anawayika mʼnyumba imene anayikapo mlonda. Iye ankawadyetsa koma sanagone nawonso. Anasungidwa kwa okha mpaka tsiku la kufa kwawo ndipo anakhala ngati akazi amasiye. Kenaka mfumu inati kwa Amasa, “Itanitsa ankhondo a Yuda kuti abwere kwa ine pasanathe masiku atatu, ndipo iwe udzakhale nawo.” Motero Amasa anakayitana Ayuda, koma anachedwa, napitirira pa nthawi imene mfumu inamuyikira. Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.” Kotero anthu a Yowabu, Akereti ndi Apeleti ndiponso asilikali onse amphamvu anapita motsogozedwa ndi Abisai. Iwo anayenda kuchokera ku Yerusalemu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri. Ali pa mwala waukulu wa ku Gibiyoni, Amasa anabwera kudzakumana nawo. Yowabu anali atavala chovala chausilikali ndipo pamwamba pa malayawo, mʼchiwuno mwake anavala lamba womangirirapo lupanga lili moyikamo mwakemo. Akuyenda linasololoka kuchoka moyikamo mwake. Yowabu anati kwa Amasa, “Kodi uli bwanji mʼbale wanga?” Kenaka Yowabu anamugwira ndevu Amasa uja ndi dzanja lake lamanja ndi kupsompsona. Amasa sanayangʼanitsitse lupanga limene linali mʼdzanja la Yowabu, ndipo Yowabu anamubaya nalo mʼmimba ndipo matumbo ake anatuluka ndi kugwera pansi. Popanda kubayanso kachiwiri, Amasa anafa. Ndipo Yowabu ndi mʼbale wake Abisai anathamangitsa Seba mwana wa Bikiri. Mmodzi mwa ankhondo a Yowabu anakayimirira pafupi ndi mtembo wa Amasa ndipo anati, “Aliyense amene amakonda Yowabu ndi aliyense amene ali wa Davide, atsatire Yowabu!” Amasa anagona pakati pa msewu atasamba magazi ake, ndipo munthuyo anaona kuti asilikali onse amayima pamenepo. Atazindikira kuti aliyense amene ankafika pamene panali Amasa amayima, iye anamuchotsa mu msewu ndi kumukokera mʼmunda ndipo anamuphimba ndi nsalu. Amasa atachotsedwa pa msewu anthu onse anapita ndi Yowabu kuthamangitsa Seba mwana wa Bikiri. Seba anadutsa mafuko onse a Israeli mpaka ku Abeli ndi Beti-Maaka ndiponso chigawo chonse cha Abeli, amene anasonkhana pamodzi ndi kumutsata iye. Ankhondo onse pamodzi ndi Yowabu anafika ndi kumuzungulira Seba mu Abeli-Beti-Maaka. Iwo anapanga mzere wa nkhondo mpaka ku mzinda, ndipo unayangʼanana ndi malo otetezera a kunja. Pamene amalimbana ndi khoma kuti aligwetse, mayi wina wanzeru anafuwula kuchokera mu mzindawo, “Tamverani! Tamverani! Muwuzeni Yowabu abwere pano kuti ndiyankhule naye.” Yowabu anayandikira kumene kunali mayiyo, ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndinu Yowabu?” Iye anayankha kuti, “Ndine.” Mayiyo anati, “Tamverani zimene mtumiki wanu akuti anene.” Yowabu anayankha kuti, “Ndikumvetsera.” Iye anapitiriza kunena kuti, “Kalekale ankanena kuti, ‘Kapeze yankho lako ku Abeli,’ ndipo nkhani imathera pamenepo. Ife ndife anthu a mtendere ndi okhulupirika mu Israeli. Inu mukufuna kuwononga mzinda umene ndi mayi mu Israeli. Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufafaniza cholowa cha Yehova?” Yowabu anayankha kuti, “Ayi ndisatero. Ine sindikufuna kuwufafaniza kapena kuwuwononga. Nkhani simeneyo ayi. Koma munthu wina wa ku dziko lamapiri la Efereimu, dzina lake Seba mwana wa Bikiri, wawukira mfumu Davide. Muperekeni munthuyo ndipo ine ndidzachoka pa mzinda uno.” Mayiyo anati kwa Yowabu, “Mutu wake tikuponyerani pa khoma pano.” Ndipo mayiyo anapita kwa anthu onse ndi malangizo ake anzeru, ndipo anadula mutu wa Seba mwana wa Bikiri ndipo anawuponya kwa Yowabu. Kotero iye analiza lipenga ndipo anthu ake anachoka pa mzindawo, aliyense nʼkubwerera kwawo. Ndipo Yowabu anabwerera kwa mfumu ku Yerusalemu. Yowabu ndiye amalamulira gulu lonse la ankhondo. Benaya mwana wa Yehoyada amalamulira Akereti ndi Apeleti. Adoramu amayangʼanira anthu ogwira ntchito ya thangata, Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika, Seva anali mlembi wa mfumu. Zadoki ndi Abiatara anali ansembe ndipo Ira wa ku Yairi anali wansembe wa Davide. Agibiyoni Abwezera Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide kunali njala kwa zaka zitatu zotsatana. Kotero Davide anapemphera kwa Yehova. Yehova anati, “Izi zachitika chifukwa chakuti Sauli ndi banja lake akanali ndi mlandu wakupha Agibiyoni.” Mfumu inayitanitsa Agibiyoni ndipo inayankhula nawo. (Tsono Agibiyoni sanali Aisraeli, koma otsala mwa Aamori. Aisraeli analumbira kuwasiya ndi moyo, koma Sauli chifukwa cha chikondi cha pa Israeli ndi Yuda, anafuna kuwawonongeratu). Davide anafunsa Agibiyoni kuti, “Kodi ine ndikuchitireni chiyani? Ndipepese bwanji kuti inu mudalitse cholowa cha Yehova?” Agibiyoni anamuyankha kuti, “Ife tilibe ufulu woti nʼkulamula Sauli ndi banja lake kuti atipatse siliva kapena golide, tilibenso ufulu woti nʼkupha wina aliyense mu Israeli.” Davide anafunsa, “Mukufuna ine ndikuchitireni chiyani?” Iwo anayankha mfumu kuti, “Tsono za munthu amene anatiwononga ndi kukonza chiwembu choti titheretu ndi kukhala wopanda malo mu Israeli, mutipatse adzukulu ake aamuna asanu ndi awiri kuti tiwaphe ndi kuwapereka pamaso pa Yehova ku Gibeya wa Sauli, wosankhidwa wa Yehova.” Choncho mfumu inati, “Ine ndidzakupatsani.” Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova. Ndipo mfumu inatenga Arimoni ndi Mefiboseti, ana aamuna awiri a Rizipa, mwana wamkazi wa Ayiwa, amene anaberekera Sauli pamodzi ndi ana asanu a Merabi mwana wamkazi wa Sauli, amene anabereka Adirieli mwana wa Barizilai Mmeholati. Iye anawapereka kwa anthu a ku Gibiyoni, amene anawapha nawayika pa phiri la Yehova. Onse asanu ndi awiri anafera limodzi. Iwo anaphedwa masiku oyamba kukolola barele. Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa anatenga chiguduli ndi kudziyalira pa mwala (pamene panali mitemboyo). Kuyambira nthawi yoyamba kukolola mpaka pamene mvula inayambanso kugwa, iye sanalole kuti mbalame zikhudze mitemboyo masana kapena nyama zakuthengo usiku. Davide atawuzidwa zimene Rizipa mwana wamkazi wa Ayiwa, mzikazi wa Sauli anachita, anapita kukatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kwa anthu a ku Yabesi Giliyadi (iwo anawatenga mwamseri kuchoka pabwalo la ku Beti-Sani, kumene Afilisti anawapachika atapha Sauli ku Gilibowa). Davide anakatenga mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani kumeneko ndiponso mafupa otayidwa a amene anaphedwa nawasonkhanitsa pamodzi. Iwo anayika mafupa a Sauli ndi mwana wake Yonatani mʼmanda a Kisi abambo ake a Sauli ku Zera mʼdziko la Benjamini, ndipo anachita zonse zimene mfumu inalamula. Atachita zimenezi, Mulungu anayankha pemphero lopempherera dzikolo. Nkhondo ndi Afilisti Nthawi inanso panali nkhondo pakati pa Afilisti ndi Aisraeli, Davide anapita ndi ankhondo ake kukamenyana ndi Afilisti ndipo iye anatopa kwambiri. Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide. Koma Abisai mwana wa Zeruya anabwera kudzapulumutsa Davide. Iye anamukantha Mfilisitiyo ndi kumupha. Pamenepo asilikali a Davide analumbira kwa iye kuti, “Inu simudzapita nafenso ku nkhondo, kuti nyale ya Israeli isadzazimitsidwe.” Patapita nthawi, panali nkhondo ina ndi Afilisti ku Gobu. Pa nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Safu, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai. Pa nkhondo inanso ndi Afilisti ku Gobu, Elihanani mwana wa Yaare-Oregimu wa ku Betelehemu anapha Goliati Mgiti, amene anali ndi mkondo ngati ndodo yowombera nsalu. Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha. Anthu anayi amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo onse anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake. Nyimbo ya Mayamiko ya Davide Davide anayimbira Yehova nyimbo iyi pamene Yehovayo anamupulumutsa mʼdzanja la adani ake onse ndiponso mʼdzanja la Sauli. Iye anati, “Yehova ndiye thanthwe langa, chitetezo changa ndi mpulumutsi wanga. Mulungu wanga ndiye thanthwe langa, mʼmene ndimathawiramo, chishango changa ndi ndodo yachipulumutso changa. Iye ndi linga langa, pothawirapo panga ndi mpulumutsi wanga. Munandipulumutsa mʼmanja mwa anthu ankhanza. “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga. “Mafunde a imfa anandizinga; mitsinje yothamanga yachiwonongeko inandiopsa kwambiri. Anandimanga ndi zingwe za ku manda; misampha ya imfa inalimbana nane. “Mʼmasautso anga ndinapemphera kwa Yehova; ndinapemphera kwa Mulungu wanga. Iye ali mʼnyumba yake, anamva mawu anga; kulira kwanga kunafika mʼmakutu ake. “Dziko lapansi linanjenjemera ndi kuchita chivomerezi, maziko a miyamba anagwedezeka; ananjenjemera chifukwa Iye anakwiya. Mʼmphuno mwake munatuluka utsi; moto wonyeketsa unatuluka mʼkamwa mwake, makala amoto anali lawilawi mʼkamwa mwake. Iye anangʼamba thambo natsika pansi; pansi pa mapazi ake panali mitambo yakuda. Iye anakwera pa Kerubi ndi kuwuluka; nawuluka ndi mphepo mwaliwiro. Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, mitambo yakuda ya mlengalenga. Mʼkuwala kumene kunali pamaso pake munkachokera makala amoto alawilawi. Yehova anabangula kumwamba ngati bingu, mawu a Wammwambamwamba anamveka ponseponse. Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa. Zigwa za mʼnyanja zinaonekera poyera, ndipo maziko a dziko lapansi anakhala poyera, Yehova atabangula mwaukali, pamene mpweya wamphamvu unatuluka mʼmphuno mwake. “Ali kumwamba, Iye anatambalitsa dzanja lake ndipo anandigwira; anandivuwula mʼmadzi ozama. Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu, adani anga amene anali amphamvu kuposa ine. Adaniwo analimbana nane pamene ndinali pa mavuto, koma Yehova anali thandizo langa. Iye anandipititsa kumalo otakasuka; anandipulumutsa chifukwa amakondwera nane. “Yehova wandithandiza molingana ndi chilungamo changa; molingana ndi makhalidwe anga abwino, Iye wandipulumutsa. Pakuti ine ndinatsata njira za Yehova; ndilibe mlandu wochoka pamaso pa Mulungu wanga. Malamulo ake onse ali pamaso panga, sindinasiye malangizo ake. Ndakhala moyo wosalakwa pamaso pake ndipo ndakhala ndi kupewa tchimo. Yehova wandipatsa mphotho molingana ndi chilungamo changa, molingana ndi makhalidwe anga abwino pamaso pake. “Kwa wokhulupirika, Inu mumaonetsa kukhulupirika kwanu, kwa anthu amakhalidwe abwino, Inu mumaonetsanso makhalidwe abwino, Kwa woyera mtima, Inu mumaonetsa kuyera mtima kwanu, koma kwa anthu achinyengo mumaonetsanso kunyansidwa nawo. Inu mumapulumutsa anthu odzichepetsa, koma maso anu amatsutsana ndi odzikuza ndipo mumawatsitsa. Inu Yehova, ndinu nyale yanga; Yehova wasandutsa mdima wanga kukhala kuwunika. Ndi thandizo lanu nditha kulimbana ndi gulu la ankhondo, ndi Mulungu wanga nditha kuchita zosatheka ndi munthu. “Kunena za Mulungu, zochita zake ndi zangwiro; mawu a Yehova alibe cholakwika. Iye ndi chishango kwa onse amene amathawira kwa iye. Mulungu wina ndi uti wofanana nanu Yehova? Ndipo ndani amene ndi Thanthwe kupatula Mulungu wathu? Ndi Mulungu amene anandipatsa mphamvu ndi kulungamitsa njira yanga. Iye amasandutsa mapazi anga kukhala ngati ambawala yayikazi; Iye amandithandiza kuyimirira pamwamba pa mapiri. Iye amaphunzitsa manja anga kuchita nkhondo; manja anga amatha kuthyola uta wachitsulo. Inu mundipatsa ine chishango chanu cha chigonjetso; mumawerama kuti mundikweze. Inu mwalimbitsa njira yanga kuti ndiyende bwino, kuti mapazi anga asaterereke. “Ine ndinathamangitsa adani anga ndi kuwakantha; sindinabwerere mpaka iwo atawonongedwa. Ndinawakantha kotheratu, ndipo sanathe kudzukanso; Iwo anagwera pansi pa mapazi anga. Inu munandipatsa ine mphamvu yochitira nkhondo; munagwaditsa adani anga pa mapazi anga. Inu muchititsa kuti adani anga atembenuke ndi kuthawa; ndipo ndinawononga adani anga. Iwo anafuwula kupempha thandizo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe owapulumutsa. Analirira kwa Yehova, koma sanawayankhe. Ine ndinawaperesa ngati fumbi la pa dziko lapansi; ndinawasinja ndipo ndinawapondaponda ngati matope a mʼmisewu. “Inu mwandipulumutsa mʼmanja mwa mitundu ya anthu; Inu mwandisunga kuti ndikhale mtsogoleri wa anthu a mitundu ina. Anthu amene sindikuwadziwa ali pansi pa ulamuliro wanga. Alendo amadzipereka okha pamaso panga; akangomva za ine, amandigonjera. Iwo onse anataya mtima; anatuluka mʼmalinga awo akunjenjemera. “Yehova ndi wamoyo! Litamandidwe Thanthwe langa. Akuzike Mulungu, Thanthwe, Mpulumutsi wanga! Iye ndi Mulungu amene amabwezera chilango, amene amayika anthu a mitundu yonse pansi pa ulamuliro wanga, amene amandimasula mʼmanja mwa adani anga. Inu munandikuza kuposa adani anga; munandilanditsa mʼmanja mwa anthu ankhanza. Choncho ine ndidzakutamandani Inu Yehova, pakati pa anthu a mitundu ina; ndidzayimba nyimbo zotamanda dzina lanu. “Iye amapereka chipambano chachikulu kwa mfumu yake, amaonetsa kukoma mtima kwa wodzozedwa wake, kwa Davide ndi zidzukulu zake kwamuyaya.” Mawu Otsiriza a Davide Nawa mawu otsiriza a Davide: “Mawu a Davide mwana wa Yese, mawu a munthu amene wakwezedwa ndi Wammwambamwamba, munthu wodzozedwa ndi Mulungu wa Yakobo, woyimba nyimbo za Israeli: “Mzimu wa Yehova unayankhula kudzera mwa ine; mawu ake anali pakamwa panga. Mulungu wa Israeli anayankhula, Thanthwe la Israeli linati kwa ine: ‘Pamene munthu alamulira anthu mwachilungamo, pamene alamulira moopa Mulungu, amakhala ngati kuwala kwa mmamawa, mmawa wopanda mitambo, monga kuwala pamene mvula yaleka kugwa imene imameretsa udzu mʼnthaka.’ “Kodi banja langa silolungama pamaso pa Mulungu? Kodi Iye sanachite pangano losatha ndi ine, lokonzedwa ndi lotetezedwa mbali zonse? Kodi sadzakwaniritsa chipulumutso changa, ndi kundipatsa chokhumba changa chilichonse? Koma anthu oyipa ndiwo ayenera kutayidwa kunja ngati minga, imene sitengedwa ndi manja. Aliyense amene wayikhudza mingayo amayidula pogwiritsa ntchito chigwandali kapena ndodo ya mkondo; nayitentha pa moto.” Ankhondo Otchuka a Davide Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yosebu-Basebeti wa ku Takemoni mkulu wa atsogoleri a ankhondo atatu. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 800 nthawi imodzi. Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi. Monga mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu a Davide, iye anali ndi Davide pamene anazunza Afilisti amene anasonkhana ku Pasi-Damimu kuchita nkhondo. Kenaka ankhondo a Israeli anabwerera mʼmbuyo. Koma iye anayima osasuntha ndipo anakantha Afilisti mpaka mkono wake unatopa ndipo unakanirira ku lupanga lake. Yehova anapereka chigonjetso chachikulu pa tsiku limenelo. Asilikali anabwerera kwa Eliezara, kukatenga katundu wa anthu ophedwa. Wotsatana naye anali Sama mwana wa Age Mharari. Pamene Afilisti anasonkhana pamalo pamene panali munda wa mphodza, ankhondo a Israeli anathawa Afilistiwo. Koma Sama anayima pakati pa mundawo. Iye anawuteteza nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa. Pa nthawi yokolola, atatu mwa atsogoleri makumi atatu anabwera kwa Davide ku phanga la Adulamu, pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” Choncho anthu amphamvu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo. Abisai mʼbale wa Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300, choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja. Kodi iyeyo sanali wolemekezeka koposa? Iye anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango. Ndipo iye anakanthanso Mwigupto wamkulu msinkhu. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe. Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja. Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu aja, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza. Mʼgulu la anthu makumi atatu aja munalinso awa: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, Sama Mharodi, Elika Mherodi, Helezi Mpaliti, Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiezeri wa ku Anatoti, Sibekai Mhusati, Zalimoni Mwahohi, Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini, Benaya Mpiratoni, Hidayi wa ku zigwa za Gaasi. Abi-Aliboni Mwaribati, Azimaveti Mbarihumi, Eliyahiba Msaaliboni, ana a Yaseni, Yonatani, mwana wa Sama Mharari, Ahiamu mwana wa Sarari Mharari, Elifeleti mwana wa Ahasibai Mmaakati, Eliamu mwana wa Ahitofele Mgiloni, Heziro wa ku Karimeli, Paarai Mwaribi, Igala mwana wa Natani wa ku Zoba, mwana wa Hagiri, Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri, ndi Uriya Mhiti. Onse pamodzi analipo 37. Davide Awerenga Ankhondo Nthawi inanso Yehova anawakwiyira Aisraeli ndipo anawutsa mtima wa Davide kuti awavutitse ndipo anati, “Pita kawerenge Aisraeli ndi Ayuda.” Choncho mfumu inati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali nawo. “Pitani pakati pa mafuko onse a Israeli kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba kuti mukawerenge anthu omenya nkhondo ndi cholinga choti ndidziwe chiwerengero chawo.” Koma Yowabu anayankha mfumu kuti, “Yehova Mulungu wanu achulukitse ankhondo anu kukhala miyandamiyanda, ndipo alole inu mbuye wanga mfumu mudzazione zimenezi. Koma nʼchifukwa chiyani inu mbuye wanga mfumu mukufuna kuchita zimenezi?” Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu ndi atsogoleri a ankhondo. Choncho anachoka pamaso pa mfumu kupita kukawerenga anthu omenya nkhondo mu Israeli. Atawoloka Yorodani, iwo anamanga misasa yawo pafupi ndi Aroeri kummwera kwa mzinda wa ku chigwa ndipo kenaka iwo anapita ku dziko la Gadi mpaka ku Yazeri. Iwo anapita ku Giliyadi ndi ku chigwa cha Tahitimu Hodisi ndipo anapitirira mpaka ku Dani Yaani ndi madera ozungulira Sidoni. Kenaka iwo anapita molunjika linga la ku Turo ndi ku mizinda yonse ya Ahivi ndi Akanaani. Pomaliza anapita ku Beeriseba ku Negevi wa ku Yuda. Atayendayenda mʼdziko lonse anabwerera ku Yerusalemu patapita miyezi isanu ndi inayi ndi masiku makumi awiri. Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa mfumu: Mu Israeli munali anthu 800,000 amphamvu amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga ndipo mu Yuda munali anthu 500,000. Davide anatsutsika mu mtima mwake atatha kuwerenga anthuwo ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono Yehova, ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.” Davide asanadzuke mmawa mwake mawu a Yehova anafika kwa mneneri Gadi, mlosi wa Davide kuti, “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ” Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa iye, “Kodi mungakonde kuti mʼdziko mwanu mukhale njala kwa zaka zitatu? Kapena kuti mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu? Kapena kuti mʼdziko muno mukhale mliri kwa masiku atatu? Tsopano, ganizirani bwino ndipo musankhe chomwe mudzamuyankhe amene wandituma.” Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ife atilange ndi Yehova pakuti chifundo chake ndi chachikulu, koma ndisalangidwe ndi anthu.” Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, kuyambira mmawa mpaka pa nthawi imene anafuna mwini wake, ndipo unapha anthu 70,000 kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Pamene mngelo anatambasula dzanja lake kuti awononge Yerusalemu, Yehova anamva chisoni chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. Davide ataona mngelo amene ankakantha anthu uja, anati kwa Yehova, “Ine ndi amene ndachimwa. Ine mʼbusa ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Langani ineyo pamodzi ndi banja langa.” Davide Amanga Guwa la Nsembe Tsiku limenelo Gadi anapita kwa Davide ndi kukanena kuti, “Pitani kamangeni guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi.” Ndipo Davide anapita monga momwe Yehova anamulamulira kudzera mwa Gadi. Arauna atayangʼana ndi kuona mfumu ndi anthu ake akubwera kumene kunali iye, iyeyo anatuluka ndi kuwerama pamaso pa mfumu mpaka nkhope yake kugunda pansi. Arauna anati, “Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mfumu mwabwera kwa mtumiki wanu?” Davide anayankha kuti, “Kudzagula malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe kuti mliri uli pa anthuwa usiye.” Arauna anati kwa Davide, “Mbuye wanga mfumu mutenge chilichonse chimene chikukondweretseni ndi kuchipereka nsembe. Nazi ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, nazi zopunthira tirigu ndi magoli angʼombe kuti zikhale nkhuni. Inu mfumu, Arauna akupereka zonsezi kwa inu mfumu.” Arauna anatinso kwa iye, “Yehova Mulungu wanu akuvomerezeni.” Koma mfumu inayankha Arauna kuti, “Ayi, Ine ndikunenetsa kuti ndikulipira. Sindidzapereka kwa Yehova Mulungu wanga nsembe yopsereza imene sindinavutikire.” Kotero Davide anagula malo wopunthira tiriguwo ndi ngʼombe ndipo anapereka kwa Araunayo masekeli asiliva makumi asanu. Davide anamanga guwa lansembe la Yehova pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Ndipo Yehova anayankha pempherolo mʼmalo mwa dziko lonse, ndipo mliri unatha pa Aisraeli.