- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 2 PETRO Kalata Yachiwiri ya Petro 2 Petro 2 Pet KALATA YACHIWIRI YA PETRO Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu. Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu. Kudziwa za Mayitanidwe ndi za Kusankhidwa Kwathu Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa. Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale. Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kukhala Oyera Mtima Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano. Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani, chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu. Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse. Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake. Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.” Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija. Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa. Aphunzitsi Onyenga Koma panalinso aneneri onama pakati pa Aisraeli, monga padzakhalanso aphunzitsi onyenga pakati panu. Iwo adzalowetsa mwamseri ziphunzitso zonama ndi zowononga, nadzakana Ambuye amene anawawombola, ndipo motero adzadziyitanira okha chiwonongeko mwadzidzidzi. Ambiri adzatsata njira zawo zochititsa manyazi ndipo chifukwa cha iwowa, anthu adzanyoza njira ya choonadi. Pofuna kupeza chuma, aphunzitsiwa adzakudyerani chuma chanu pokuwuzani nkhani zopeka. Chiweruzo chawo chinakonzedwa kale, ndipo chikuwadikira. Pakuti Mulungu sanalekerere angelo atachimwa paja, koma anawaponya mʼndende, nawayika mʼmaenje amdima, kuwasunga kuti adzaweruzidwe. Iye sanalekerere dziko lapansi kalelo, koma anapulumutsa Nowa, mlaliki wa chilungamo, ndi anthu ena asanu ndi awiri atadzetsa chigumula pa dziko lapansi kwa anthu akhalidwe losapembedza Mulunguyo. Mulungu anaweruza mizinda ya Sodomu ndi Gomora nayiwononga ndi moto, kuti ikhale chitsanzo cha zimene zidzachitikira anthu osapembedza Mulungu. Koma Iye anapulumutsa Loti, munthu wolungama, amene ankavutika ndi khalidwe lonyansa la anthu oyipa. (Pakuti munthu wolungamayo, pokhala pakati pawo tsiku ndi tsiku ankavutika mu mtima ndi makhalidwe awo oyipa amene ankawaona ndi kuwamva). Tsono mutha kuona kuti Ambuye amadziwa kuwapulumutsa kwake pa mayesero anthu opembedza. Amadziwanso kusunga osalungama kuti alangidwe mpaka tsiku la chiweruzo. Makamaka amene amatsata zilakolako zonyansa zathupi nanyoza ulamuliro. Anthu amenewa ndi odzikuza, ndipo otsata chifuniro cha iwo eni, sasamala za munthu, saopa kuchitira chipongwe zolengedwa za mmwamba. Komatu ngakhale angelo, amene ali akulu ndi amphamvu kuwaposa, sayankhula za chipongwe pobweretsa chiweruzo pa iwo kuchokera kwa Ambuye. Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa. Iwo adzalangidwa chifukwa cha zoyipa zimene anachita. Koma chimene chimawakomera ndi kumangochita zokondweretsa thupi masanasana. Iwo ali ngati mawanga ndi zilema. Podya nanu pamodzi amakondwera kuchita za chinyengo. Ndi maso awo odzaza ndi chigololo, salekeza kuchimwa. Amanyengerera anthu osakhazikika. Iwo ndi akatswiri pa dyera ndi chuma, ndipo ndi ana otembereredwa! Iwo anasiya njira yolungama ndipo anapatuka kutsata njira ya Baalamu mwana wa Beori, amene anakonda malipiro a chosalungama. Koma anadzudzulidwa chifukwa cha kulakwa kwakeko. Bulu, nyama imene siyankhula, inayankhula ngati munthu kuletsa misala ya mneneriyo. Anthu amenewa ali ngati akasupe wopanda madzi, ndiponso ngati nkhungu yowuluzidwa ndi mphepo yamkuntho. Mulungu wawasungira mdima wandiweyani. Pakuti anayankhula mawu opanda pake ndi onyada, ndipo ndi zilakolako zoyipa za thupi amanyenga anthu amene angopulumuka kumene pakati pa anzawo oyipa. Amawalonjeza ufulu, pomwe iwo eni ndi akapolo a zizolowezi zowononga. Pajatu munthu amakhala kapolo wa chilichonse chimene chikumulamulira. Ngati anapulumuka ku zodetsa za dziko lapansi podziwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, pambuyo pake nagwidwanso ndi kugonjetsedwa ndi zomwezo, potsiriza adzakhala oyipa kuposa mmene analili poyamba. Kukanakhala bwino akanapanda kudziwa njira ya chilungamo, koposa ndi kuyileka atadziwa lamulo loyera limene Mulungu anawapatsa. Kwa iwo miyambi iyi ndi yoona, “Galu wabwerera ku masanzi ake,” ndipo, “Nkhumba imene inasamba, yakunkhunizikanso mʼmatope.” Kubwera kwa Ambuye Inu okondedwa, iyi ndi kalata yanga yachiwiri kwa inu. Ine ndalemba makalata onse awiri kuti ndikukumbutseni ndi kukutsitsimutsani ndi cholinga choti muzilingalira moyenera. Ndikufuna kuti mukumbukire mawu amene anayankhulidwa kale ndi aneneri oyera mtima ndiponso lamulo limene Ambuye ndi Mpulumutsi wathu analipereka kudzera mwa atumwi. Poyamba mudziwe kuti mʼmasiku otsiriza kudzafika anthu onyoza, adzanyoza ndi kutsata zilakolako zawo zoyipa. Iwo adzati, “Kodi suja Ambuye analonjeza kuti adzabweranso? Nanga ali kuti? Lija nʼkale anamwalira makolo athu, koma zinthu zonse zili monga anazilengera poyamba paja.” Koma iwo akuyiwala dala kuti Mulungu atanena mawu, kumwamba kunakhalapo ndipo analenga dziko lapansi ndi madzi. Ndi madzinso achigumula, dziko lapansi la masiku amenewo linawonongedwa. Dziko la kumwamba ndi lapansi la masiku ano akulisunga ndi mawu omwewo kuti adzalitentha ndi moto. Akuzisunga mpaka tsiku limene adzaweruza ndi kuwononga anthu onse osapembedza Mulungu. Koma abale okondedwa, musayiwale chinthu chimodzi ichi: Kuti pamaso pa Ambuye tsiku limodzi lili ngati zaka 1,000, ndipo zaka 1,000 zili ngati tsiku limodzi! Ambuye sazengereza kuchita zimene analonjeza, monga ena amaganizira. Iwo akukulezerani mtima, sakufuna kuti aliyense awonongeke, koma akufuna kuti aliyense alape. Koma tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala. Pa tsikuli zinthu zakumwamba zidzachoka ndi phokoso lalikulu. Zinthu zonse zidzawonongedwa ndi moto, ndipo dziko lapansi ndi zonse zili mʼmenemo zidzapsa. Popeza kuti zinthu zonse zidzawonongedwa motere, kodi inu muyenera kukhala anthu otani? Muyenera kukhala moyo wachiyero ndi opembedza Mulungu pamene mukuyembekezera tsiku la Mulungu ndi kufulumiza kufika kwake. Pa tsiku limeneli zinthu zakumwamba zidzawonongedwa ndi moto, ndipo zidzasungunuka ndi kutentha. Koma ife tikudikira kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano, zimene Mulungu analonjeza, mʼmene chilungamo chidzakhalamo. Chomwecho okondedwa, popeza inu mukudikira zimenezi, chitani changu kuti mukhale wopanda chilema kuti mukhale pa mtendere ndi Iye. Zindikirani kuti kuleza mtima kwa Ambuye kukutanthauza chipulumutso, monga momwe mʼbale wathu wokondedwa Paulo anakulemberaninso ndi nzeru zimene Mulungu anamupatsa. Iye walemba chimodzimodzi makalata ake onse, kuyankhula za zinthu izi. Mʼmakalata ake mumakhala zinthu zina zovuta kuzimvetsa, zimene anthu osadziwa ndi osakhazikika amazipotoza, monga amachita ndi malemba ena onse, potero akudziwononga okha. Nʼchifukwa chake, abale okondedwa, popeza mukuzidziwa kale zimenezi, chenjerani kuti musatengeke ndi zolakwa za anthu osaweruzika, mungagwe ndi kuchoka pamalo otetezedwa. Koma kulani mu chisomo ndi mʼchidziwitso cha Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. Kwa Iye kukhale ulemerero tsopano mpaka muyaya. Ameni.