- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
2 MAFUMU
2 Mafumu
2 Mafumu
2 Maf
2 Mafumu
Yehova Alanga Ahaziya
Atamwalira Ahabu, Mowabu anawukira Israeli. Ndipo Ahaziya anagwa kuchokera pa khonde la chipinda chake chammwamba ku Samariya, ndipo anavulala kwambiri. Choncho iye anatuma amithenga nawawuza kuti, “Pitani mukafunse kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, ngati ndichire matendawa.”
Koma mngelo wa Yehova anawuza Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi amithenga a mfumu ya ku Samariya ndipo ukawafunse kuti, ‘Kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake inu mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni?’ Tsono Yehova akuti, ‘Iweyo sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ” Ndipo Eliya ananyamuka.
Amithenga aja atabwerera kwa mfumu, mfumuyo inawafunsa kuti, “Chifukwa chiyani mwabwerera?”
Iwo anayankha kuti, “Munthu wina anabwera kudzakumana nafe, ndipo anatiwuza kuti, bwererani kwa mfumu imene inakutumani ndipo mukayiwuze kuti, ‘Yehova akuti, kodi popeza kulibe Mulungu ku Israeli, nʼchifukwa chake mukupita kukafunsa nzeru kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni? Tsono sudzadzuka pa bedi wagonapo. Udzafa ndithu!’ ”
Mfumu inafunsa amithengawo kuti, “Kodi munthu amene anabwera kudzakumana nanuyo ndi kukuwuzani zimenezi amaoneka bwanji?”
Iwo anayankha kuti, “Munthuyo anavala zovala zaubweya ndi lamba wachikopa mʼchiwuno mwake.”
Mfumu inati, “Munthu ameneyo ndi Eliya wa ku Tisibe.”
Pamenepo mfumu inatuma mtsogoleri wa ankhondo ndi anthu ake makumi asanu kwa Eliya. Mtsogoleriyo anapita kwa Eliya, amene anali atakhala pamwamba pa phiri, ndipo anati, “Munthu wa Mulungu, mfumu ikuti, ‘Tsikani!’ ”
Eliya anayankha mtsogoleriyo kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu makumi asanu akowo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
Zitachitika izi, mfumu inatumanso mtsogoleri wina pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleriyo anati kwa Eliya, “Munthu wa Mulungu, zimene mfumu ikunena ndi izi, ‘Tsikani msangamsanga!’ ”
Eliya anayankha kuti, “Ngati ndine munthu wa Mulungu, moto utsike kuchokera kumwamba, ukupsereze iwe pamodzi ndi anthu ako makumi asanuwo!” Pomwepo moto unatsikadi kuchokera kumwamba ndipo unapsereza mtsogoleriyo pamodzi ndi anthu akewo.
Ndipo mfumu inatumanso mtsogoleri wachitatu pamodzi ndi asilikali ake makumi asanu. Mtsogoleri wachitatuyu anakwera pa phiripo ndi kugwada pamaso pa Eliya. Iye anayankhula mopemba kuti, “Munthu wa Mulungu, chonde musandiwononge ineyo pamodzi ndi atumiki makumi asanu anuwa! Taonani, moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kupsereza atsogoleri awiri pamodzi ndi anthu awo onse. Koma tsopano musawononge moyo wanga!”
Mngelo wa Yehova anati kwa Eliya, “Pita naye, usamuope.” Choncho Eliya ananyamuka natsika naye limodzi kupita kwa mfumu.
Eliya anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chiyani munatumiza amithenga kwa Baala-zebubu, mulungu wa ku Ekroni, kukafunsa ngati muti muchire? Kodi mu Israeli mulibe Mulungu woti nʼkukuyankhani funso lanu? Choncho, popeza mwachita izi, simudzadzuka pamene mwagonapo; mudzafa ndithu.’ ” Motero Ahaziya anafadi, monga mwa mawu a Yehova amene Eliya anayankhula.
Tsono popeza Ahaziya analibe mwana, Yoramu analowa ufumu mʼmalo mwake mʼchaka chachiwiri cha Yehoramu mwana wa Yehosafati mfumu ya ku Yuda. Ntchito zina zonse zimene Ahaziya anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
Eliya Atengedwa Kupita Kumwamba
Yehova ali pafupi kutenga Eliya kupita kumwamba mu kamvuluvulu, Eliya ndi Elisa anali pa ulendo wopita ku Giligala. Eliya anawuza Elisa kuti, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Beteli.”
Koma Elisa anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Beteli.
Ana a aneneri a ku Beteli anabwera kwa Elisa namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”
Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma musakambe zimenezi.”
Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yeriko.”
Koma Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapita ku Yeriko.
Ana a aneneri amene anali ku Yeriko anapita kwa Elisa, namufunsa kuti, “Kodi ukudziwa kuti lero Yehova akuchotsera mbuye wako?”
Elisa anayankha kuti, “Inde ndikudziwa, koma inu musakambe zimenezi.”
Ndipo Eliya anati kwa Elisa, “Iwe khala pano pakuti Yehova wandituma kuti ndipite ku Yorodani.”
Elisa anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Motero awiriwo anapitirira ulendo wawo.
Anthu makumi asanu mwa ana a aneneri anawatsatira nayima chapatali moyangʼanana nawo ndipo Eliya ndi Elisa anayima mʼmphepete mwa Yorodani. Eliya anatenga chovala chake nachipinda, napanda madzi ndi chovalacho. Madziwo anagawikana, ena kwina ena kwina, ndipo awiriwo anawoloka powuma.
Atawoloka, Eliya anati kwa Elisa, “Ndifotokozere, ndikuchitire chiyani ndisanachotsedwe pamaso pako?”
Elisa anayankha kuti, “Ndikupemphani kuti mundipatse magawo awiri a mphamvu za mzimu wanu wa uneneri.”
Eliya anati, “Wapempha chinthu chapatali, komabe ukandiona pamene ndikuchotsedwa pamaso pako, mphamvu wapemphayi idzakhala yako, koma ukapanda kundiona sizidzachitika.”
Akuyenda ndi kumakambirana, mwadzidzidzi galeta lamoto ndi akavalo amoto anaonekera ndi kuwasiyanitsa awiriwo, ndipo Eliya anapita kumwamba mʼkamvuluvulu. Elisa anaona zimenezi ndipo anafuwula kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi anthu ake okwera pa akavalo!” Ndipo Elisa sanamuonenso Eliyayo. Pamenepo Elisa anagwira zovala zake nazingʼamba pakati.
Iye anatola chovala cha Eliya chomwe chinagwa nabwerera ndi kukayima mʼmphepete mwa Yorodani. Ndipo Elisa anatenga chovala chomwe chinagwa kuchokera kwa Eliya napanda nacho madzi. Iye anafunsa kuti, “Ali kuti Mulungu wa Eliya?” Atapanda madzi, madziwo anagawika pakati, ena kwina ena kwina, ndipo iye anawoloka.
Ndipo ana a aneneri ochokera ku Yeriko atamuona anati, “Mzimu wa Eliya wakhazikika pa Elisa.” Ndipo anapita kukakumana naye nagwada ndi kuweramitsa mitu yawo pansi pamaso pake. Ndipo anawuza Elisa kuti, “Ife atumiki anu tili ndi anthu amphamvu makumi asanu. Aloleni apite kuti akafunefune mbuye wanu. Mwina Mzimu wa Yehova wamutenga ndi kukamuponya ku phiri lina kapena ku chigwa china.”
Elisa anayankha kuti, “Ayi, musawatume.”
Koma anamukakamizabe mpaka Elisayo anachita manyazi moti sakanatha kukana. Choncho iye anati, “Atumizeni.” Ndipo anatumiza anthu makumi asanu amene anakafunafuna Eliya kwa masiku atatu koma sanamupeze. Atabwerera kwa Elisa (chifukwa anali akanali ku Yeriko), iye anawawuza kuti, “Kodi sindinakuwuzeni kuti musapite?”
Kuchiritsidwa kwa Madzi
Anthu a mu mzindamo anati kwa Elisa, “Mbuye wathu, taonani mzinda uno uli pamalo pabwino, monga mukuoneramu, koma madzi ake ndi oyipa, nthaka yakenso ndi yosabereka.”
Iye anati, “Patseni mbale yatsopano ndipo muyikemo mchere.” Ndipo anabweretsa mbaleyo kwa iye.
Kenaka Elisa anapita ku kasupe wa madziwo, nathiramo mchere mʼkasupemo nati, “Yehova akuti, ‘Ndachiritsa madzi awa. Madzi amenewa sadzabweretsanso imfa kapena kuchititsa kuti nthaka ikhale yosabereka.’ ” Kotero madziwo ndi abwino mpaka lero, molingana ndi mawu amene Elisa anayankhula.
Kusekedwa kwa Elisa
Kuchokera kumeneko Elisa anapita ku Beteli. Ndipo pamene ankayenda mu msewu, anyamata ena achichepere anatuluka mu mzindamo nʼkumamuseka. Iwo ankanena kuti, “Choka iwe, wachidazi! Choka iwe wachidazi” Iye anatembenuka nawayangʼana ndipo anawatemberera mʼdzina la Yehova. Nthawi yomweyo panatulukira zimbalangondo ziwiri kuchokera kuthengo, ndi kuphapo anyamata 42. Ndipo iye anapita ku phiri la Karimeli. Pochoka kumeneko anabwerera ku Samariya.
Kuwukira kwa Mowabu
Yoramu mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya mʼchaka cha 18 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda ndipo analamulira zaka khumi ndi ziwiri. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova koma sizinafanane ndi zimene anachita abambo ndi amayi ake. Iye anachotsa fano la mwala la Baala limene abambo ake anapanga. Komabe anawumirira kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo sanafune kuwaleka.
Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna. Koma atamwalira Ahabu, mfumu ya ku Mowabu inawukira mfumu ya ku Israeli. Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse. Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?”
Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.”
Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
Mfumu inafuwula kuti, “Nʼchiyani chomwe chikutichitikira! Kodi Yehova wasonkhanitsa mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu?”
Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?”
Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
Yehosafati anati, “Yehova amayankhula kudzera mwa iye.” Choncho mfumu ya ku Israeli pamodzi ndi Yehosafati ndiponso mfumu ya ku Edomu anapita kwa Elisa.
Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.”
Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe. Koma tsopano ndiyitanireni munthu wodziwa kuyimba bwino zeze.”
Munthuyo akuyimba zeze, mphamvu ya Yehova inafika pa Elisa, ndipo anati, “Yehova akuti, ‘Kumbani ngalande mʼchigwa chonse.’ Pakuti Yehova akunena kuti, ‘Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe chigwa ichi chopanda madzi chidzadzaza ndi madzi, ndipo inu mudzamwa pamodzi ndi ngʼombe zanu ndiponso nyama zanu zonse.’ Izi ndi zosavuta pamaso pa Yehova. Ndipo adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu. Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”
Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.
Tsono nʼkuti Amowabu onse atamva kuti mafumu abwera kudzachita nawo nkhondo. Kotero, anayitana munthu aliyense, wamkulu ndi wamngʼono amene ankatha kugwira chida chankhondo ndipo anakayima ku malire a dziko lawo. Amowabu atadzuka mmamawa, dzuwa likuwala pa madziwo, anaona madziwo akuoneka wofiira ngati magazi patsogolo pawo. Ndipo iwo anati, “Taonani magazi! Mafumu aja amenyana okhaokha ndipo aphana. Amowabu, tsopano ndi nthawi yofunkha!”
Koma Amowabu atafika ku misasa ya Israeli, Aisraeli ananyamuka ndi kumenyana nawo mpaka anathawa. Ndipo Aisraeli analowa mʼdzikolo ndi kupha Amowabu. Aisraeli anagumula mizinda yawo ndipo munthu aliyense anaponya mwala pa munda uliwonse wachonde mpaka utadzaza ndi miyala. Iwo anatseka akasupe onse amadzi ndiponso anadula mtengo wabwino uliwonse. Mzinda wa Kiri Hareseti wokha ndiye unatsala wotetezedwa koma anthu oponya miyala anawuzungulira nawuthiranso nkhondo.
Mfumu ya ku Mowabu itaona kuti nkhondo ikumulaka, inatenga anthu 700 a malupanga kuti athawe modutsa mfumu ya ku Edomu, koma inalephera. Choncho inatenga mwana wake wamwamuna woyamba kubadwa, amene akanalowa ufumu mʼmalo mwake, ndi kumupereka nsembe pa khoma la mzinda. Zimenezi zinachititsa kuti mkwiyo ndi ukali wa Amowabu ukule kwambiri pa Aisraeli ndipo Aisraeliwo anathawa nabwerera ku dziko la kwawo.
Mafuta a Mkazi Wamasiye
Mkazi wa mmodzi mwa ana a aneneri anafuwula kwa Elisa kuti, “Mtumiki wanu, mwamuna wanga wamwalira ndipo inu mukudziwa kuti ankaopa Yehova. Koma tsopano munthu amene mwamuna wanga anakongolako zinthu zake, akubwera kudzatenga ana anga awiri aamuna kuti akhale akapolo ake.”
Elisa anayankha mayiyo kuti, “Kodi ufuna ndikuchitire chiyani? Tandiwuza uli ndi chiyani mʼnyumba mwako?”
Mayiyo anayankha kuti, “Mdzakazi wanu alibe kanthu kalikonse koma timafuta pangʼono chabe.”
Elisa anati, “Pita kabwereke mitsuko yonse yopanda kanthu kwa anzako. Usakabwereke mitsuko yochepa. Kenaka ukalowe mʼnyumba mwako ndi kudzitsekera iwe ndi ana ako. Mukakatero mukakhuthulire mafuta mʼmitsuko yonseyo, ndipo mtsuko uliwonse ukadzaza muzikawuyika pambali.”
Mayi uja anachoka kwa Elisa nakadzitsekera ndi ana ake. Anthu anabweretsa mitsuko kwa iye ndipo ankathiramo mafuta. Mitsuko yonse itadzaza, mayiyo anawuza mwana wake kuti, “Bweretsa mtsuko wina.”
Koma iye anayankha kuti, “Mitsuko yonse yatha.” Pamenepo mafuta analeka kutuluka.
Mayiyo anapita nakamuwuza munthu wa Mulungu amene anamuyankha kuti, “Pita, kagulitse mafutawo ndipo ukabweze ngongole ija. Ndalama zotsalazo zikakhale zako ndi ana ako.”
Elisa Aukitsa Mwana wa Mayi wa ku Sunemu
Tsiku lina Elisa anapita ku Sunemu. Kumeneko kunkakhala mayi wina wachuma amene anawumiriza Elisa kuti adye chakudya. Choncho nthawi iliyonse imene Elisa amadutsa kumeneko, ankayima ndi kudya. Mayiyo anawuza mwamuna wake kuti, “Taonani, ine ndikudziwa kuti munthu amene amadutsa pano nthawi zambiriyu ndi munthu woyera wa Mulungu. Tiyeni timumangire kachipinda kakangʼono pa denga la nyumbayi ndi kumuyikiramo bedi ndi tebulo, mpando ndi nyale. Akabwera kuno azikhala mʼmenemo.”
Tsiku lina pamene Elisa anafika ku Sunemu, iye anakalowa mʼchipinda chake chija nagona mʼmenemo. Iye anati kwa mtumiki wake Gehazi, “Muyitane Msunemuyu.” Ndipo anapita kukamuyitana mayiyo, ndipo anabwera nayima pamaso pa Elisa. Elisa anati kwa Gehazi, “Muwuze mayiyo kuti, ‘Wavutika potichitira zonsezi. Nanga tsopano ifeyo tikuchitire chiyani? Kodi ukufuna kuti tikadziwitse mfumu kapena mtsogoleri wa ankhondo zimene watichitirazi?’ ”
Mayiyo anayankha kuti, “Ine ndimakhala mwamtendere pakati pa abale anga.”
Elisa anafunsanso Gehazi kuti, “Kodi tingamuchitire chiyani?”
Gehazi anati, “Ndithu, mayiyu alibe mwana ndipo mwamuna wake ndi wokalamba.”
Pamenepo Elisa anati, “Muyitane.” Choncho Gehazi anamuyitana, ndipo iye anabwera nayima pa khomo. Elisa anati kwa mayiyo, “Nthawi ngati yomwe ino chaka chamawa, udzakhala utanyamula mwana wamwamuna mʼmanja mwako.”
Mayiyo anatsutsa zimenezi nanena kuti, “Ayi mbuye wanga. Inu munthu wa Mulungu, musanamize mdzakazi wanu!”
Koma mayi uja anakhala woyembekezera, ndipo chaka chotsatiracho, nthawi ngati yomweyo anabereka mwana wamwamuna monga momwe Elisa anamuwuzira.
Mwana uja anakula, ndipo tsiku lina anapita kwa abambo ake amene anali ndi anthu odula tirigu. Mwanayo anafuwula kwa abambo ake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mayo! Mutu wanga ine!”
Abambo akewo anawuza wantchito wake kuti, “Munyamule ndi kukamupereka kwa amayi ake.” Wantchito uja atamunyamula ndi kumupereka kwa amayi ake. Mwanayo anakhala pa miyendo ya amayi akeyo mpaka masana, ndipo pambuyo pake anamwalira. Mayiyo ananyamula mwanayo nakamugoneka pa bedi la munthu wa Mulungu uja. Kenaka anatseka chitseko iye nʼkuchokapo.
Iye anayitanitsa mwamuna wake namuwuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi kuti ndipite mofulumira kwa munthu wa Mulungu nʼkubwererako.”
Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.”
Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
Mayiyo anamangirira chishalo pa bulu ndipo anawuza wantchito wake kuti, “Yendetsa bulu mofulumira. Usachepetse liwiro pokhapokha nditakuwuza.” Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli.
Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo! Thamanga msanga ukakumane naye ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi muli bwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Kodi mwana wanu ali bwino?’ ”
Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”
Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”
Tsono mayiyo anati, “Mbuye wanga, kodi ine ndinakupemphani mwana? Kodi sindinakuwuzeni kuti musandinamize?”
Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”
Koma mayi wake wa mwana uja anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Choncho Elisa ananyamuka natsatira mayiyo.
Gehazi anatsogola nakagoneka ndodoyo pa nkhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena kugwedezeka kuonetsa kuti ali moyo. Choncho Gehazi anabwerera kukakumana ndi Elisa ndipo anamuwuza kuti, “Mwanayo sanatsitsimuke.”
Ndipo Elisa atafika ku nyumbako, taonani, mwanayo anali wakufa atamugoneka pa bedi lake. Elisa analowa mʼnyumbamo natseka chitseko. Anali awiri okha mʼchipindamo ndipo iye anapemphera kwa Yehova. Kenaka anakwera pa bedi ndi kumugonera mwanayo, pakamwa pake panakhudzana ndi pakamwa pa mwanayo, maso ake anakhudzana ndi maso a mwanayo, ndipo manja ake anakhudzana ndi manja a mwanayo. Pamene ankadzitambalitsa yekha pa mwanayo, thupi la mwanayo linayamba kufunda. Elisa anatembenuka nayenda uku ndi uku kamodzi mʼchipindamo ndipo kenaka anakweranso pa bedi nagoneranso mwanayo. Mwanayo anayetsemula kasanu ndi kawiri ndipo anatsekula maso ake.
Elisa anayitana Gehazi ndipo anati, “Muyitane Msunemuyo.” Ndipo anaterodi. Mayiyo atabwera, Elisa anati, “Tenga mwana wako.” Mayiyo analowa, nagwada pa mapazi a Elisa, naweramitsa mutu wake pansi. Kenaka ananyamula mwana wake natuluka.
Imfa mu Mʼphika
Elisa anabwerera ku Giligala ndipo ku dera limenelo kunali njala. Elisa akukumana ndi ana a aneneri, anati kwa mtumiki wake, “Ika mʼphika waukulu pa moto ndipo uwaphikire chakudya anthu awa.”
Mmodzi mwa ana aneneriwo anapita kuthengo kukafuna ndiwo ndipo anakapeza mpesa wakuthengo. Iye anathyolako zipatso zake nadzaza nsalu yake. Atabwerera, anazidula zipatsozo naziyika mu mʼphika, ngakhale kuti panalibe amene ankazidziwa. Anawapakulira anthu chakudyacho, koma atayamba kudya, anthuwo anafuwula kuti, “Inu munthu wa Mulungu muli imfa mu mʼphikamu!” Ndipo sakanatha kudya chakudyacho.
Elisa anati, “Bweretsani ufa.” Iye anathira ufa mu mʼphikamo ndipo anati, “Perekani chakudyachi kwa anthu kuti adye.” Ndipo mu mʼphikamo munalibenso zoopsa.
Kudyetsa Anthu 100
Munthu wina wochokera ku Baala-Salisa anabwera atamutengera munthu wa Mulungu malofu a barele makumi awiri opangidwa kuchokera ku zokolola zoyamba kucha, pamodzinso ndi ngala zatsopano za tirigu. Elisa anati kwa munthuyo, “Apatse anthu kuti adye.”
Mtumiki wake anafunsa kuti, “Kodi ndikachigawe motani chakudyachi kwa anthu 100?”
Koma Elisa anamuwuzanso kuti, “Apatse anthu adye. Pakuti izi ndi zimene Yehova akunena kuti, ‘Iwo adzadya chakudyachi ndipo china chidzatsalako.’ ” Tsono iye anachipereka kwa anthuwo ndipo anadya china nʼkutsalako, molingana ndi mawu a Yehova.
Naamani Achiritsidwa Khate Lake
Tsono Naamani anali mtsogoleri wa gulu lankhondo a mfumu ya ku Aramu. Iye anali munthu wodalirika pamaso pa mbuye wake ndipo anali wokondedwa kwambiri, chifukwa kudzera mwa iye Yehova anapambanitsa Aaramu. Anali msilikali wolimba mtima, koma anali ndi khate.
Tsono magulu a Aaramu anapita ku nkhondo ndipo anakagwira ukapolo mtsikana wamngʼono wa ku Israeli, ndipo ankatumikira mkazi wa Naamani. Mtsikanayo anawuza mkazi wa Naamani kuti, “Mbuye wanga akanapita kukaonana ndi mneneri amene amakhala ku Samariya, akanachiritsidwa khate lawo.”
Naamani anapita kwa mbuye wake kukamuwuza zomwe mtsikana wochokera ku Israeli ananena. Mfumu ya ku Aramu inayankha kuti, “Iwe uyenera kupita. Ine ndilembera kalata mfumu ya ku Israeli.” Choncho Naamani ananyamuka kupita ku Samariya, atatenga ndalama za siliva 30,000, ndalama zagolide 6,000 ndiponso zovala khumi za pa chikondwerero. Kalata imene anapita nayo kwa mfumu ya ku Israeli inali ndi mawu awa: “Taonani, ndikutumiza Naamani mtumiki wanga pamodzi ndi kalatayi kwa inu kuti mumuchiritse khate lake.”
Mfumu ya ku Israeli itangowerenga kalatayo, inangʼamba mkanjo wake ndipo inati, “Kodi ine ndine Mulungu? Kodi ndingathe kupha kapena kupereka moyo? Chifukwa chiyani munthu ameneyu wanditumizira munthu woti ndimuchiritse khate lake? Taonani, iyeyu akungofuna kuti apeze chifukwa choyambanirana nane!”
Elisa munthu wa Mulungu atamva kuti mfumu ya ku Israeli yangʼamba mkanjo wake, anatumiza uthenga uwu: “Chifukwa chiyani mwangʼamba mkanjo wanu? Mutumizeni munthuyo kwa ine ndipo iyeyo adzadziwa kuti muli mneneri mu Israeli.” Choncho Naamani anapita pamodzi ndi akavalo ake ndi magaleta nakayima pa khomo la nyumba ya Elisa. Elisa anatumiza uthenga kwa iye woti, “Pita, kasambe kasanu ndi kawiri mu mtsinje wa Yorodani, thupi lako lidzachira ndi kukhalanso monga kale ndipo udzayeretsedwa.”
Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa. Kodi Abana ndi Faripara, mitsinje ya ku Damasiko, siyoposa mitsinje ina yonse ya ku Israeli? Kodi sindikanasamba mʼmitsinje imeneyo ndi kuyeretsedwa?” Kotero anatembenuka nachoka ali wokwiya kwambiri.
Antchito ake anamuyandikira namufunsa kuti, “Abambo anga, mneneri akanakulamulani chinthu chachikulu, kodi inu simukanachita? Nanga nʼzovuta motani zomwe mneneri wanena kuti ‘Kasambeni ndipo mudzayeretsedwa!’ ” Choncho Naamani anapita ku Yorodani nakadzimiza mʼmadzimo kasanu nʼkawiri, monga momwe munthu wa Mulungu anamuwuzira. Thupi lake linakhalanso monga kale ndipo linakhala losalala ngati la kamnyamata.
Pamenepo Naamani ndi atumiki ake onse anabwerera kwa munthu wa Mulungu uja. Naamani anayima pamaso pa Elisa ndipo anati, “Tsopano ndikudziwa kuti kulibe Mulungu wina pa dziko lonse lapansi koma mu Israeli mokha. Chonde, tsopano landirani mphatso ya mtumiki wanu.”
Mneneri anayankha kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene ine ndimamutumikira, sindidzalandira zimenezi.” Ndipo ngakhale Naamani anamukakamiza, iye anakanabe.
Naamani anati, “Ngati inu simulandira, chonde lolani mtumiki wanu kuti atengeko dothi lokwanira kunyamula abulu awiri, popeza mtumiki wanu sadzaperekanso nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa mulungu wina koma Yehova. Koma Yehova andikhululukire ine pa chinthu ichi: Pamene mbuye wanga alowa mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni ine ndimapita naye ndipo ndimakagwada naye limodzi. Pamene ndikugwada mʼnyumba ya mapemphero ya Rimoni, Yehova azikhululukira mtumiki wanu pa chinthu chimenechi.”
Elisa anati, “Pita mu mtendere.”
Choncho anachoka nayenda pangʼono. Koma Gehazi, mtumiki wa Elisa munthu wa Mulungu, anaganiza mu mtima mwake kuti, “Taonani, mbuye wanga wamulekerera Naamani Mwaramuyu, posalandira zomwe anabweretsa. Pali Yehova wamoyo, ine ndimuthamangira ndipo ndikatengako zinthu kwa iye.”
Choncho Gehazi anamuthamangira Naamani uja. Naamani ataona Gehazi akumuthamangira, anatsika mʼgaleta lake ndi kukakumana naye. Iye anafunsa Gehazi kuti, “Kodi nʼkwabwino?”
Gehazi anayankha kuti, “Inde nʼkwabwino. Mbuye wanga wandituma kuti ndidzakuwuzeni kuti, ‘Anyamata awiri mwa ana a aneneri angondipeza kumene kuchokera ku dziko la mapiri la Efereimu. Chonde apatseniko ndalama za siliva 3,000 ndi zovala ziwiri za pa phwando.’ ”
Naamani anati, “Kuli bwino utenge ndalama zasiliva 6,000.” Iye anakakamiza Gehazi kuti alandire, ndipo kenaka anamanga matumba awiri a ndalama zasiliva pamodzi ndi zovala zinayi za pa mphwando. Naamani anazipereka kwa antchito ake awiri ndipo anazinyamula nayenda patsogolo pa Gehazi. Gehazi atafika ku phiri, anawalanda antchito aja zinthu zija nazibisa mʼnyumbamo. Iye anawawuza anthu aja kuti abwerere ndipo anapita. Kenaka analowa mʼnyumbamo nakayima pamaso pa mbuye wake Elisa.
Elisa anafunsa kuti, “Kodi Gehazi unali kuti?”
Iye anayankha kuti, “Mtumiki wanu sanapite kwina kulikonse.”
Koma Elisa anati kwa Gehazi, “Kodi mzimu wanga sunali nawe pamene munthu uja anatsika mʼgaleta lake ndi kukumana nawe? Kodi ino ndi nthawi yolandira ndalama, kapena kulandira zovala, mitengo ya olivi, minda ya mpesa, nkhosa, ngʼombe kapena antchito aamuna kapena antchito aakazi? Khate la Naamani lidzakumatirira iwe ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.” Ndipo Gehazi anachoka pamaso pa Elisa ali ndi khate lotuwa ngati phulusa.
Nkhwangwa Iyandama pa madzi
Ana a aneneri anati kwa Elisa, “Taonani malo amene timakhala ndi inu atichepera kwambiri. Tiloleni tipite ku Yorodani kumene aliyense wa ife akadule mtengo umodzi, kuti timange malo woti tizikhalamo.”
Ndipo Elisa anati, “Pitani.”
Mmodzi wa iwo anati, “Chonde mulole kutsagana nawo atumiki anu.”
Elisa anayankha kuti, “Ndipita nanu.” Ndipo anapita nawo.
Anapita ku Yorodani nayamba kudula mitengo. Pamene wina ankadula mtengo, nkhwangwa yake inaguluka nigwera mʼmadzi. Iye anafuwula kuti, “Mayo! Mbuye wanga! Popeza ndi yobwereka!”
Ndipo munthu wa Mulungu uja anafunsa, “Yagwera pati?” Pamene anamuonetsa malowo, Elisa anadula kamtengo nakaponya pamenepo, ndipo nkhwangwayo inayandama. Elisa anati, “Itenge.” Ndipo munthuyo anatambalitsa dzanja lake nayitenga.
Elisa Achititsa Khungu Ankhondo a ku Aramu
Tsono mfumu ya ku Aramu inali pa nkhondo ndi Israeli. Itakambirana ndi atsogoleri ake ankhondo inati, “Ndidzamanga misasa yanga pamalo akutiakuti.”
Munthu wa Mulungu anatumiza mawu kwa mfumu ya ku Israeli kuti “Musamale podutsa malo akuti, chifukwa Aaramu akupita kumeneko.” Choncho mfumu ya ku Israeli inatuma anthu kumalo kumene munthu wa Mulunguyo ananena. Nthawi ndi nthawi Elisa ankachenjeza mfumu, kotero kuti ankakhala tcheru ku malo amenewo.
Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri mfumu ya ku Aramu. Mfumuyo inayitanitsa atsogoleri ake ankhondo ndipo inawafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze munthu amene pakati pathu pano ali mbali ya mfumu ya ku Israeli?”
Mmodzi mwa atsogoleri a ankhondowo anati, “Palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu, inu mbuye wanga, koma Elisa mneneri amene ali ku Israeli amawuza mfumu ya ku Israeli mawu enieni amene inu mumayankhula ku chipinda kwanu.”
Choncho mfumu inalamula kuti, “Pitani, kafufuzeni kumene akukhala kuti ine nditume anthu kukamugwira.” Anthuwo anabweretsa mawu oti, “Taonani, Elisa ali ku Dotani.” Ndipo mfumu inatumizako magaleta ndi akavalo ndiponso gulu lankhondo lamphamvu. Anapita usiku nakawuzungulira mzindawo.
Mtumiki wa munthu wa Mulungu atadzuka mmamawa ndi kutuluka panja, gulu la ankhondo pamodzi ndi akavalo ndi magaleta anali atazungulira mzindawo. Mtumikiyo anafunsa kuti, “Kalanga mbuye wanga, tidzachita chiyani?”
Mneneri anamuyankha kuti, “Usachite mantha. Amene ali mbali yathu ndi ambiri kupambana amene ali mbali yawo.”
Ndipo Elisa anapemphera kuti, “Inu Yehova tsekulani maso ake kuti aone.” Pamenepo Yehova anatsekula maso a mtumikiyo, ndipo anayangʼana naona kuti phiri lonse linali lodzaza ndi akavalo ndi magaleta a moto atazungulira Elisa.
Pamene adaniwo ankabwera kudzalimbana naye, Elisa anapemphera kwa Yehova kuti, “Achititseni khungu anthu awa.” Kotero Yehova anawachititsa khungu monga anapemphera Elisa.
Elisa anawawuza ankhondowo kuti, “Njira si imeneyi ndipo mzinda sumenewunso. Tsateni, ndipo ndidzakutengerani kwa munthu amene mukumufunayo.” Ndipo anawatengera ku Samariya.
Atalowa mu mzinda wa Samariya, Elisa anati, “Yehova tsekulani maso a anthu awa kuti aone.” Choncho Yehova anatsekula maso awo ndipo anangoona kuti ali mʼkati mwenimweni mwa Samariya.
Mfumu ya ku Israeli itawaona, inafunsa Elisa kuti, “Abambo anga, kodi ndiwaphe? Kodi ndiwaphe?”
Elisa anayankha kuti, “Musawaphe. Kodi mungaphe anthu amene munawagwira pogwiritsa ntchito lupanga ndi uta? Apatseni chakudya ndi madzi kuti adye ndi kumwa kenaka apite kwa mbuye wawo.” Choncho anawakonzera mphwando lalikulu, ndipo atatsiriza kudya ndi kumwa, anawatumiza kwawo ndipo anabwerera kwa mbuye wawo. Kotero magulu a ankhondo a ku Aramu analeka kuthira nkhondo dziko la Israeli.
Njala mu Mzinda wa Samariya
Patapita nthawi, Beni-Hadadi mfumu ya Aramu anasonkhanitsa gulu lake lonse la ankhondo, napita kukazungulira mzinda wa Samariya. Mu mzinda wa Samariya munali njala yoopsa. Ndipo taonani, Aaramu anazungulira mzindawu kwa nthawi yayitali kotero kuti mutu wa bulu ankawugulitsa ndalama za siliva 80, ndipo magalamu 200 a zitosi za nkhunda ankawagulitsa pa mtengo wa masekeli asanu.
Pamene mfumu inkayenda pa khoma la mzindawo, mayi wina anafuwulira mfumuyo kuti, “Thandizeni mbuye wanga mfumu!”
Mfumu inayankha kuti, “Ngati Yehova sakuthandiza iwe, ine thandizo lako ndingalipeze kuti? Kuchokera ku malo opunthira tirigu kodi? Kuchokera kumalo opsinyira mphesa kodi?” Pamenepo mfumuyo inafunsa mayiyo kuti, “Kodi chakuvuta nʼchiyani?”
Iye anayankha kuti, “Mayi uyu anandiwuza kuti, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye lero, ndipo mawa tidzadya mwana wangayu.’ Choncho tinaphika mwana wanga ndi kumudya. Tsiku lotsatira lakelo ine ndinati, ‘Bweretsa mwana wako kuti timudye,’ koma iye anabisa mwana wakeyo.”
Mfumu itamva mawu a mayiyo, inangʼamba mkanjo wake. Pamene inkayenda pa khoma, anthu anayangʼana, ndipo anaona zovala zamʼkati, pakuti anavala chiguduli. Mfumuyo inati, “Mulungu andilange, andilange kwambiri ndikapanda kudula mutu wa Elisa mwana wa Safati lero!”
Tsono Elisa nʼkuti atakhala mʼnyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Mfumu inatuma munthu wina kuti imutsogolere, koma asanafike, Elisa anawuza akuluakuluwo kuti, “Kodi simukuona momwe wopha munthu uja watumizira munthu wina kuti adzadule mutu wanga? Taonani mthengayo akafika, mutseke chitseko ndipo muchigwiritsitse kuti asalowe. Kodi ndikumvawo pambuyo pake si mgugu wa mbuye wake?”
Elisa akuyankhulabe ndi anthuwo, taonani, wamthengayo anafika kwa iye. Ndipo mfumu inati, “Mavuto amenewa ndi ochokera kwa Yehova. Kodi nʼchifukwa chiyani ine ndiyenera kudikira thandizo lochokera kwa Yehova?”
Ndipo Elisa anati, “Mverani mawu a Yehova. Yehova akuti, ‘Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.’ ”
Mtsogoleri amene mfumu inkamudalira anati kwa munthu wa Mulungu, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?”
Elisa anamuyankha kuti, “Taona, iweyo udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.”
Akhate Anayi Awulula za Kuthawa kwa Aaramu
Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa? Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.”
Iwo ananyamuka ndi kachisisira kupita ku msasa wa Aaramu. Atafika mʼmalire a msasa, taonani, sanapeze munthu ndi mmodzi yemwe, pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!” Choncho ananyamuka nathawa ndi kachisisira ndipo anasiya matenti, akavalo ndi abulu awo. Iwo anasiya msasa wawo momwe unalili nathawa kupulumutsa miyoyo yawo.
Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso.
Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.”
Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.” Alonda a pa chipata aja analengeza uthengawu kwa okhala mʼnyumba yaufumu.
Mfumu inadzuka usiku ndipo inawuza atsogoleri ake a ankhondo kuti, “Ndikukuwuzani zimene Aaramu atichitira ife. Akudziwa kuti tikufa ndi njala; kotero achoka mu msasa wawo kukabisala kuthengo ndi kuti, ‘Iwowa atuluka ndithu, ndipo ife tidzawagwira amoyo ndi kulowa mu mzindamo.’ ”
Mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo anayankha kuti, “Chonde uzani anthu ena atenge akavalo asanu amene atsala mu mzinda muno. Taonani, zomwe zingawachitikire zidzakhala zofanana ndi zomwe zingachitikire ena onse amene atsala. Inde iwo adzangokhala ngati Aisraeli ena onse amene awonongeka kale. Choncho tiyeni tiwatume akafufuze zomwe zachitika.”
Choncho anasankha magaleta awiri pamodzi ndi akavalo ake, ndipo mfumu inawatuma kuti alondole gulu lankhondo la Aaramu. Mfumuyo inalamula oyendetsa akavalowo kuti, “Pitani kaoneni.” Anthuwa anawalondola mpaka ku Yorodani, ndipo taonani, mʼnjira monse munali zovala zokhazokha ndi zinthu zimene Aaramu ankazitaya pamene ankathawa mofulumira. Ndipo amithengawo anabwerera ndi kudzafotokozera mfumu. Tsono anthu a mu Samariya anatuluka nakafunkha ku msasa wa Aaramu. Kotero kuti makilogalamu atatu a ufa ankawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele ankawagulitsanso pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, monga momwe ananenera Yehova.
Tsono mfumu inayika mtsogoleri amene ankamudalira uja kuti akhale woyangʼanira pa chipata ndipo anthu anamupondaponda ku chipata kuja, ndipo anafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu ananenera mfumu itapita ku nyumba yake. Zinachitika molingana ndi zomwe ananena munthu wa Mulungu zija kuti “Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.”
Mtsogoleriyu ananena kwa munthu wa Mulungu kuti, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Munthu wa Mulungu anamuyankha kuti, “Iwe udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.” Ndipo izi ndi zomwe zinamuchitikiradi mtsogoleriyu, pakuti anthu anamupondaponda pa chipata ndipo anafa.
Mayi wa ku Sunemu Atenganso Munda wake
Ndipo Elisa anawuza mayi amene anamuukitsira mwana wake kuti, “Choka kuno pamodzi ndi banja lako ndipo ukakhale kulikonse ukufuna, chifukwa Yehova akubweretsa njala ya zaka zisanu ndi ziwiri mʼdziko muno.” Mayiyo ananyamuka nachita zimene munthu wa Mulungu ananena. Iye pamodzi ndi banja lake anachoka nakakhala ku dziko la Afilisti zaka zisanu ndi ziwiri.
Zitatha zaka zisanu ndi ziwirizo anabwera kuchokera ku dziko la Afilisti ndipo anapita kwa mfumu kukafunsa za nyumba yake ndi munda wake. Ndipo mfumu inkayankhula ndi Gehazi, mtumiki wa munthu wa Mulungu kuti, “Tandiwuza zinthu zikuluzikulu zimene Elisa wachita.” Pamene Gehazi ankayiwuza mfumuyo momwe Elisa anaukitsira anthu akufa, mayi amene mwana wake Elisa anamuukitsa kwa akufayo analowa kudzafunsa mfumu za nyumba yake ndi munda wake.
Gehazi anati, “Mbuye wanga mfumu, mayi wake ndi uyu ndipo mwana wakeyo ndi uyu amene Elisa anamuukitsa kwa akufa.” Mfumu inafunsa mayiyo za nkhaniyi ndipo iye anayifotokozera mfumuyo.
Ndipo mfumu inasankha munthu woti ayendetse nkhani yake ndipo inati, “Mubwezereni zonse zimene zinali zake, kuphatikizapo phindu lonse lochokera mʼmunda wake, kuyambira tsiku limene anachoka mpaka tsopano lino.”
Hazaeli Apha Beni-Hadadi
Elisa anapita ku Damasiko, ndipo Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu ankadwala. Mfumuyo itawuzidwa kuti, “Munthu wa Mulungu wabwera kuno kuchokera kutali,” inawuza Hazaeli kuti, “Tenga mphatso ndipo pita ukakumane ndi munthu wa Mulungu. Ukandifunsire kwa Yehova kudzera mwa iye kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”
Choncho Hazaeli anapita kukakumana ndi Elisa, atasenzetsa ngamira 40 mphatso za zinthu zosiyanasiyana zabwino kwambiri za ku Damasiko. Iye analowa mʼnyumba ya Elisa ndi kuyima pamaso pake, ndipo anati, “Mwana wanu Beni-Hadadi wandituma kuti ndidzakufunseni kuti, ‘Kodi ndidzachira matenda angawa?’ ”
Elisa anayankha kuti, “Pita ndipo ukamuwuze kuti, ‘Udzachira ndithu,’ koma Yehova wandionetsa kuti adzafabe.” Elisa anamuyangʼana kwambiri Hazaeli mpaka anachita manyazi. Pamenepo munthu wa Mulungu anayamba kulira.
Hazaeli anafunsa kuti, “Mbuye wanga mukulira chifukwa chiyani?”
Elisa anayankha kuti, “Chifukwa ndikudziwa choyipa chimene udzachitira Aisraeli. Udzatentha mizinda yawo ya chitetezo, udzapha anyamata awo ndi lupanga, udzaphwanyitsa pansi makanda awo ndiponso udzatumbula mimba za akazi awo oyembekezera.”
Ndipo Hazaeli anati, “Kodi kapolo wanune, amene ndine wonyozeka ngati galu, ndingathe bwanji kuchita chinthu chachikulu chotere?”
Elisa anayankha kuti, “Yehova wandionetsa kuti iwe udzakhala mfumu ya ku Aramu.”
Choncho Hazaeli anasiyana ndi Elisa ndi kubwerera kwa mbuye wake. Beni-Hadadi atafunsa kuti, “Elisa wakuwuza chiyani?” Hazaeli anayankha kuti, “Elisa wandiwuza kuti inu mudzachira ndithu.” Koma mmawa mwake Hazaeli anatenga nsalu yokhuthala ndi kuyiviyika mʼmadzi ndipo anaphimba nayo nkhope ya mfumu, kotero mfumuyo inafa. Hazaeli analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehoramu Mfumu ya ku Yuda
Chaka chachisanu cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya ku Israeli, Yehosafati ali mfumu ya ku Yuda, Yehoramu mwana wake anakhala mfumu ya Ayuda. Yehoramu analowa ufumu ali ndi zaka 32, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zisanu ndi zitatu. Iye anatsatira khalidwe la mafumu a ku Israeli, monga mmene linachitira banja la Ahabu, popeza iye anakwatira mwana wa Ahabu. Yehoramu anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Komabe, chifukwa cha mtumiki wake Davide, Yehova sanafune kuwononga Yuda popeza Yehova analonjeza Davide kuti adzamupatsa nyale pamodzi ndi zidzukulu zake mpaka muyaya.
Pa nthawi ya Yehoramu, Edomu anawukira ulamuliro wa Yuda ndipo anadzisankhira mfumu. Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Ndipo iye anakantha Aedomu amene anamuzungulira pamodzi ndi oyendetsa magaleta ake usiku. Koma ankhondo ake anathawa napita ku misasa yawo. Mpaka lero lino Edomu ndi wowukira Yuda. Nthawi yomweyo mzinda wa Libina unawukiranso.
Ndipo ntchito zina za Yehoramu ndi zonse zomwe anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Choncho Yehoramu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ahaziya Mfumu ya ku Yuda
Mʼchaka cha khumi ndi chiwiri cha Yoramu mwana wa Ahabu mfumu ya Israeli, Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Ahaziya anali ndi zaka 22 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu chaka chimodzi. Amayi ake anali Ataliya, chidzukulu cha Omiri mfumu ya Israeli. Iye anatsatira makhalidwe a banja la Ahabu ndipo anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga linachitira banja la Ahabu, pakuti anali mkamwini wa banja la Ahabu.
Ahaziya anapita pamodzi ndi Yoramu mwana wa Ahabu kukachita nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya Aramu ku Ramoti Giliyadi. Aaramu anavulaza Yoramu. Choncho mfumu Yoramu inabwerera ku Yezireeli kuti ikachire mabala ake amene Aaramu anamuvulaza ku Rama pa nkhondo yake ndi Hazaeli mfumu ya Aramu.
Tsono Ahaziya mwana wa Yehoramu mfumu ya ku Yuda anapita ku Yezireeli kuti akamuone Yoramu mwana wa Ahabu, popeza nʼkuti akudwala.
Yehu Adzozedwa Ufumu wa ku Israeli
Mneneri Elisa anayitanitsa mmodzi mwa ana a aneneri, namuwuza kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga botolo la mafuta mʼdzanja lako ndipo upite ku Ramoti Giliyadi. Ukakafika kumeneko, ukafunefune Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi. Ukapite kwa iye, ukamuchotse pakati pa anzake ndi kukamulowetsa mʼchipinda chamʼkati. Ndipo ukatenge botololi ndi kuthira mafuta pa mutu wake ndipo ukanene kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ Kenaka ukatsekule chitseko ndi kuthawa ndipo usakachedwe!”
Choncho mneneri wachinyamatayo anapita ku Ramoti Giliyadi. Atafika ku Giliyadiko anapeza atsogoleri a ankhondo ali pa msonkhano. Iye anati, “Mtsogoleri, ine ndili ndi uthenga wanu.”
Ndipo Yehu anafunsa kuti, “Uthengawo ndi wa yani pakati pathu?”
Mneneriyo anayankha kuti, “Ndi wa inuyo, mtsogoleri.”
Yehu anayimirira nakalowa mʼnyumba. Pamenepo mneneriyo anakhuthulira mafuta pamutu pa Yehu ndipo ananena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndikukudzoza kukhala mfumu ya Israeli, anthu a Yehova. Uyenera kuwononga nyumba ya mbuye wako Ahabu ndipo ndidzabwezera imfa ya atumiki anga, aneneri ndiponso imfa ya atumiki ena onse a Yehova amene anaphedwa ndi Yezebeli. Banja lonse la Ahabu lidzatheratu. Ndidzachotsa munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu kaya ndi kapolo kapena mfulu. Ndidzachititsa kuti banja la Ahabu lifanane ndi banja la Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati banja la Baasa mwana wa Ahiya. Kunena za Yezebeli, agalu adzamudya ku dera la Yezireeli ndipo palibe amene adzamuyike mʼmanda.’ ” Kenaka mneneriyo anatsekula chitseko nʼkuthawa.
Yehu atatuluka kupita kumene kunali atsogoleri anzake, mmodzi mwa iwo anamufunsa kuti, “Kodi zonse zili bwino? Kodi munthu wamisala uja anabwera kudzatani kwa iwe?”
Yehu anayankha kuti, “Iwe ukumudziwa munthu uja ndiponso ukudziwa zomwe amayankhula.”
Atsogoleri aja anati, “Ukunama! Tiwuze.”
Yehu anati, “Zimene wandiwuza ndi izi: ‘Yehova akuti: Ine ndakudzoza iwe kukhala mfumu ya Israeli.’ ”
Atsogoleri aja mofulumira anatenga zofunda zawo naziyala pansi pa makwerero kuti Yehu akhalepo. Kenaka analiza lipenga, nafuwula kuti, “Yehu ndiye mfumu!”
Yehu Apha Yoramu ndi Ahaziya
Choncho Yehu mwana wa Yehosafati, mwana wa Nimisi, anachitira chiwembu Yoramu. (Nthawi imeneyi nʼkuti Yoramu ndi Aisraeli onse akuteteza Ramoti Giliyadi kwa Hazaeli mfumu ya ku Aramu, koma nʼkuti Yoramu atabwerera ku Yezireeli kuti akachire mabala amene Aaramu anamuvulaza pa nkhondo ndi Hazaeli mfumu ya ku Aramu.) Yehu anati, “Ngati mukugwirizana nazo zimenezi, wina aliyense asatuluke mu mzinda muno kupita kukafotokoza nkhaniyi ku Yezireeli.” Pamenepo Yehu anakwera galeta lake, napita ku Yezireeli, chifukwa Yoramu anali akupumula kumeneko ndipo Ahaziya, mfumu ya ku Yuda, nʼkuti ali komweko kudzamuona.
Mlonda amene ankayimirira pa nsanja yolondera mzinda wa Yezireeli ataona gulu lankhondo la Yehu likuyandikira, anafuwula kuti, “Ndikuona gulu lankhondo likubwera.”
Yoramu analamula kuti, “Peza munthu wokwera kavalo, mutume kuti akakumane nawo ndi kuwafunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”
Choncho munthu wokwera kavalo anapita kukakumana ndi Yehu ndipo anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”
Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
Mlonda uja anakafotokoza kwa mfumu kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwerera.”
Choncho mfumu inatumanso munthu wina wachiwiri wokwera kavalo. Atafika kwa anthuwo iye anati, “Mfumu ikufunsa kuti, ‘Kodi mukubwera mwamtendere?’ ”
Yehu anayankha kuti, “Kodi iwe nkhani ya mtendere yakukhudza bwanji? Tiye, zinditsata pambuyo panga.”
Mlonda uja anakanenanso kuti, “Wamthenga uja wakafika kwa anthuwo koma sakubwereranso. Kuyendako kukukhala ngati kwa Yehu mwana wa Nimisi, iye amayenda ngati munthu wamisala.”
Yoramu analamula kuti, “Konzani galeta langa.” Ndipo atakonza galeta lake, Yoramu mfumu ya Israeli ndi Ahaziya mfumu ya ku Yuda anakwera nʼkutuluka mu mzindamo, aliyense atakwera galeta lake, kukakumana ndi Yehu. Iwo anakumana ndi Yehu pa munda umene unali wa Naboti, wa ku Yezireeli. Yoramu ataona Yehu anafunsa kuti, “Yehu, kodi wabwera mwamtendere?”
Yehu anayankha kuti, “Pangakhale bwanji mtendere pamene zopembedza mafano zonse zilipo ndiponso ufiti wa amayi ako Yezebeli uli ponseponse?”
Yoramu anatembenuka, nathawa akufuwula kwa Ahaziya kuti, “Ahaziya, anthuwa atiwukira!”
Pamenepo Yehu anakoka uta wake ndipo analasa Yoramu kumsana pakati pa mapewa. Muviwo unakalasa mtima wake ndipo anagwa pansi mʼgaleta lakelo. Yehu anawuza Bidikara, mtsogoleri wa galeta lake kuti, “Munyamule ndipo ukamuponye mʼmunda umene unali wa Naboti wa ku Yezireeli, chifukwa kumbukira mmene iwe ndi ine tinkayenda pambuyo pa Ahabu abambo ake, kuti Yehova ananeneratu za iye kuti, ‘Zoonadi dzulo ndinaona magazi a Naboti ndi magazi a ana ake, akutero Yehova, ndipo Ine ndidzakubwezera ndithu choyipa chimenechi pa munda womwe uno, akutero Yehova.’ Tsono munyamule ndipo ukamuponye mʼmundamo, potsatira zimene Yehova ananena.”
Ahaziya mfumu ya ku Yuda ataona zimene zinachitika, anathawira ku Beti Hagani. Yehu anamuthamangitsa, uku akufuwula kuti, “Mupheninso!” Iwo anamuvulaza ali mʼgaleta lakelo pa njira yopita ku Guri pafupi ndi Ibuleamu, koma iye anathawira ku Megido ndipo anakafera kumeneko. Antchito ake anamunyamulira mʼgaleta kupita naye ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. (Mʼchaka cha khumi ndi chimodzi cha ufumu wa Yoramu mwana wa Ahabu, Ahaziya anakhala mfumu ya ku Yuda).
Kuphedwa kwa Yezebeli
Kenaka Yehu anapita ku Yezireeli. Yezebeli atamva zimene zinachitika, anapaka zodzikometsera mʼmaso, naluka tsitsi lake, namasuzumira pa zenera. Pamene Yehu ankalowa pa chipata iye anafunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere, iwe Zimuri, munthu wopha mbuye wako?”
Yehu anakweza maso nayangʼana pa zenera, ndipo anafuwula kuti, “Kodi ndani ali mbali yanga? Ndani?” Anthu ofulidwa awiri kapena atatu anayangʼana Yehu pansipo. Yehu anawawuza kuti, “Muponyeni pansi!” Motero anamuponya pansi ndipo magazi ake ena anafalikira pa khoma ndi pa akavalo pamene ankamupondaponda.
Yehu analowa mʼnyumba yaufumu ndipo anadya ndi kumwa. Kenaka iye anati, “Kamutoleni mkazi wotembereredwayo, ndipo kamuyikeni mʼmanda, popeza ndi mwana wa mfumu.” Koma atapita kuti akamuyike mʼmanda, sanapeze kanthu kupatula chibade cha mutu wokha, mapazi ake ndi manja ake. Choncho iwo anabwerera kwa Yehu ndi kukamufotokozera kuti, “Mawu amene Yehova anayankhula kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe ndi awa: Pa munda wa ku Yezireeli agalu adzadya mtembo wa Yezebeli. Mtembo wa Yezebeli udzakhala ngati zinyalala pa munda wa ku Yezireeli, kotero kuti palibe amene adzathe kunena kuti, ‘Uyu ndi Yezebeli.’ ”
Kuphedwa kwa Banja la Ahabu
Tsono Ahabu anali ndi ana aamuna 70 a ku Samariya. Ndipo Yehu analemba makalata nawatumiza ku Samariya kwa atsogoleri a mu mzinda wa Yezireeli, kwa akuluakulu ndiponso kwa amene ankalera ana a Ahabu, nati, “Inu mukangolandira kalatayi, popeza ana a mbuye wanu ali ndi inu ndiponso muli ndi magaleta ndi akavalo, mzinda wotetezedwa ndi zida zankhondo, sankhani mwana wa mbuye wanu amene ndi wooneka bwino ndiponso woyenera, mulowetseni ufumu wa abambo ake. Kenaka muchite nkhondo kuteteza nyumba ya mbuye wanu.”
Koma anthuwo anachita mantha kwambiri ndipo anati, “Taonani, mafumu awiri sanathe kulimbana naye, nanga ife tingathe bwanji?”
Choncho woyangʼanira nyumba ya mfumu, bwanamkubwa wa mzinda, akuluakulu ena ndiponso olera anawo anatumiza uthenga uwu kwa Yehu: “Ife ndife atumiki anu ndipo tidzachita chilichonse chomwe mutiwuze. Sitidzasankha munthu wina aliyense kukhala mfumu ndipo chitani chimene mukuganiza kuti nʼchabwino kwa inu.”
Ndipo Yehu anawalembera kalata yachiwiri yonena kuti, “Ngati inu muli mbali yanga ndi kuti mudzandimvera, mudule mitu ya ana a mbuye wanu ndipo mubwere nayo kwa ine ku Yezireeli mawa nthawi ngati yomwe ino.”
Tsono ana a mfumu onse 70 anali pamodzi ndi akuluakulu a mu mzindamo, amene ankawalera. Kalatayo itafika, anthuwo anatenga ana a mfumu 70 aja ndi kuwapha onse. Anayika mitu yawo mʼmadengu ndi kuyitumiza ku Yezireeli kwa Yehu. Mthenga uja atafika, anamuwuza Yehu kuti, “Abweretsa mitu ya ana a mfumu.”
Ndipo Yehu analamula kuti, “Unjikani mituyo mʼmilu iwiri pa chipata cha mzinda ndipo ikhale pamenepo mpaka mmawa.”
Mmawa mwake Yehu anatuluka. Iye anayimirira pamaso pa anthu onse ndipo anati, “Inu ndinu osalakwa. Ndine amene ndinachita chiwembu mbuye wanu ndi kumupha, koma kodi wapha anthu onsewa ndani? Koma dziwani tsono, kuti mawu amene Yehova anayankhula kunena za banja la Ahabu sadzapita padera. Yehova wachita chimene analonjeza kudzera mwa mtumiki wake Eliya.” Choncho Yehu anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Yezireeli, pamodzinso ndi akuluakulu ake onse, abwenzi ake ndiponso ansembe ake, sanasiyeko ndi mmodzi yemwe wamoyo.
Kenaka Yehu ananyamuka kupita ku Samariya. Atafika pa malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa, Yehu anakumana ndi abale ena a Ahaziya mfumu ya Yuda nawafunsa kuti, “Kodi ndinu yani?”
Iwo anayankha kuti, “Ndife abale ake a Ahaziya, ndipo tabwera kulonjera banja la mfumu ndi ana a mfumukazi.”
Yehu analamula kuti, “Atengeni amoyo!” Choncho anawatenga amoyo ndipo anakawaphera ku chitsime cha ku malo otchedwa Beti-Ekedi wa abusa; anthu onse 42. Iye sanasiyepo ndi mmodzi yemwe wamoyo.
Yehu atachoka kumeneko anakumana ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu, amene amabwera kudzakumana naye. Yehu anamulonjera nati kwa iye, “Kodi mtima wako uli bwino monga momwe mtima wanga ugwirizana nawo mtima wako?”
Yehonadabu anayankha kuti, “Inde ndikugwirizana nawe.”
Yehu anati, “Ngati ndi choncho, gwire dzanja.” Ndipo iye anaterodi, ndipo Yehu anamugwira dzanja namulowetsa mʼgaleta lake. Yehu anati, “Tiye kuno uwone mmene ndikudziperekera kwa Yehova.” Ndipo anayenda naye mʼgaleta mwake.
Yehu atafika ku Samariya, anapha onse amene anatsala a mʼbanja la Ahabu ku Samariya; anawawonongeratu potsata mawu a Yehova amene anayankhula kudzera mwa Eliya.
Aneneri a Baala Aphedwa
Ndipo Yehu anasonkhanitsa anthu onse pamodzi nawawuza kuti, “Ahabu ankatumikira Baala pangʼono chabe; Yehu adzamutumikira kwambiri. Tsopano itanani aneneri a Baala onse, atumiki ake onse ndi ansembe ake onse. Pasapezeke ndi mmodzi yemwe wotsala chifukwa ine ndidzapereka nsembe yayikulu kwa Baala. Aliyense amene alephere kubwera adzaphedwa.” Koma Yehu anachita zimenezi mwachinyengo ndi cholinga choti awononge atumiki onse a Baala.
Yehu anati, “Itanitsani msonkhano wodzalemekeza Baala.” Ndipo analengeza za msonkhanowo. Pamenepo Yehu anatumiza mawu ku dziko lonse la Israeli ndipo atumiki onse a Baala anabwera; palibe ndi mmodzi yemwe amene anatsala. Iwo anadzaza nyumba ya Baala. Nyumbayo inadzaziratu kuchokera ku khoma lina mpaka ku khoma lina. Ndipo Yehu anawuza munthu wosunga mikanjo kuti, “Bweretsa mikanjo yokwanira atumiki onse a Baala.” Ndipo iye anabweretsa mikanjoyo.
Kenaka Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu analowa mʼnyumba ya Baala. Yehu anawawuza atumiki a Baala kuti, “Yangʼanitsitsani ndipo muone kuti muno musapezeke atumiki a Yehova, koma mukhale atumiki okhawo a Baala.” Choncho Yehu analowa kukapereka nsembe zina ndi nsembe zopsereza. Nthawi iyi nʼkuti Yehu atayika anthu 80 kunja kwa nyumbayo ndi chenjezo lakuti, “Ngati wina aliyense wa inu adzathawitsa wina aliyense wa anthu amene ndayika kuti muziwayangʼanira, munthu woteroyo adzaphedwa.”
Yehu atangotsiriza kupereka nsembe yopsereza, analamula alonda ndi akulu a ankhondo kuti, “Lowani ndipo mukawaphe ndipo musalole kuti wina athawe.” Choncho iwo anawapha ndi lupanga. Alonda ndi akulu a ankhondo anaponya mitembo ya anthuwo panja ndipo anakalowa mʼkati mwenimweni mwa nyumba ya Baala. Iwo anakatulutsa mwala wopatulika umene unali mʼnyumba ya Baala ndipo anawutentha. Anawononga mwala wopatulika wa Baala ndi kugwetsa nyumba ya Baala, ndipo anthu anayisandutsa chimbudzi mpaka lero lino.
Motero Yehu anawononga Baala mu Israeli. Koma Yehuyo sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli kupembedza mafano a golide a ana angʼombe ku Beteli ndi ku Dani.
Yehova anati kwa Yehu, “Chifukwa wachita bwino pokwaniritsa kuchita zabwino pamaso panga ndipo wachitira banja la Ahabu zonse zimene zinali mʼmaganizo anga, zidzukulu zako zidzakhala pa mpando waufumu wa Israeli mpaka mʼbado wachinayi.” Komatu Yehu sanasamalire kusunga lamulo la Yehova Mulungu wa Israeli ndi mtima wake wonse. Iyeyo sanaleke machimo a Yeroboamu amene anachimwitsa nawo Israeli.
Masiku amenewo Yehova anayamba kuchepetsa dziko la Israeli. Hazaeli anagonjetsa Aisraeli, kuyambira kummawa kwa Yorodani, dziko lonse la Giliyadi (chigawo cha Gadi, Rubeni ndi Manase), kuchokera ku Aroeri pafupi ndi chigwa cha Arinoni kudutsa Giliyadi mpaka ku Basani.
Ntchito zina za Yehu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli?
Yehu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ku Samariya. Ndipo Yehowahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yehu analamulira Aisraeli ku Samariya zaka 28.
Ataliya ndi Yowasi
Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu. Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe. Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo.
Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja. Yehoyada anawalamulira kuti, “Chimene muti muchite ndi ichi: Inu magulu atatu amene muti mudzakhale pa ntchito tsiku la Sabata, gulu loyamba lidzalondera nyumba ya mfumu, gulu lachiwiri lidzalondera Chipata cha Suri, ndipo gulu lachitatu lidzalondera chipata cha kumbuyo kwa asilikali amene amasinthana polondera nyumbayo. Ndipo inu amene muli mʼmagulu ena awiri amene simugwira ntchito pa tsiku la Sabata, nonse mudzalondere mfumu ku nyumbayo. Mudzakhale mozungulira mfumuyo, munthu aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake. Wina aliyense amene adzakuyandikireni adzayenera kuphedwa. Muzikhala pafupi ndi mfumu kulikonse kumene ikupita.”
Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada. Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova. Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo.
Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!”
Ataliya atamva phokoso limene alonda ndi anthuwo amachita, anapita ku Nyumba ya Yehova kumene kunali anthuwo. Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!”
Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.” Choncho anamugwira pamene amafika pa malo amene akavalo amalowera ku nyumba ya mfumu ndipo anamuphera pamenepo.
Tsono Yehoyada anachititsa pangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu kuti adzakhala anthu a Yehova. Iye anachititsanso pangano pakati pa mfumu ndi anthu. Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo.
Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova. Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu. Choncho anthu onse a mʼdzikomo anasangalala. Ndipo mu mzindamo munakhala bata chifukwa Ataliya nʼkuti ataphedwa ndi lupanga ku nyumba ya mfumu.
Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anayamba kulamulira.
Yowasi Akonzanso Nyumba ya Yehova
Mʼchaka chachisanu ndi chiwiri cha Yehu, Yowasi anakhala mfumu, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka makumi anayi. Amayi ake anali Zibiya wa ku Beeriseba. Yowasi anachita zolungama pamaso pa Yehova masiku onse amene wansembe Yehoyada ankamulangiza. Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo opembedzerako mafanowo.
Yowasi anati kwa ansembe, “Tolerani ndalama zonse zimene zimaperekedwa monga chopereka chopatulika ku Nyumba ya Yehova, ndalama zonse zamsonkho wa munthu aliyense, ndalama zomwe munthu amapereka akalonjeza ndiponso ndalama zimene munthu amapereka mwaufulu ku Nyumba ya Yehova. Wansembe aliyense alandire ndalamazo kuchokera kwa abwenzi ake, ndipo zigwiritsidwe ntchito yokonzera chilichonse chimene chipezeke kuti ndi chowonongeka mʼnyumbayo.”
Koma pofika chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, ansembewo anali asanakonze nyumbayo. Choncho Mfumu Yowasi inayitanitsa wansembe Yehoyada ndi ansembe ena ndipo inafunsa kuti, “Chifukwa chiyani simukukonza malo owonongeka a mʼnyumbayi? Musasungenso ndalama zina zochokera kwa abwenzi anu, koma muzipereke kuti akonzere nyumbayi.” Ansembe anavomera kuti salandiranso ndalama kuchokera kwa anthu ndipo kuti sindiwo amene ati akonzenso nyumbayo.
Koma wansembe Yehoyada anatenga bokosi ndipo anabowola chivundikiro chake. Anayika bokosilo pambali pa guwa lansembe, kudzanja lamanja la aliyense amene akulowa mʼNyumba ya Yehovayo. Ansembe amene ankalondera pa khomopo ankaponya mʼbokosi ndalama zonse zimene ankabwera nazo ku nyumba ya Yehova. Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba. Ankati akadziwa kuti ndalamazo zilipo zingati, ankazipereka kwa anthu amene ankayangʼanira ntchito yokonza nyumbayo. Ndalamazo ankalipira anthu amene ankagwira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa ndi amisiri omanga nyumba, amisiri a miyala ndiponso anthu ophwanya miyala. Iwo ankagula matabwa ndi miyala yosema yokonzera Nyumba ya Yehova ndipo ankalipira zinthu zonse zofunika pokonzanso nyumbayo.
Koma ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku nyumbayo sanagulire siliva wopangira mabeseni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, malipenga kapena ziwiya zina zilizonse zagolide kapena zasiliva za ku Nyumba ya Yehova. Ndalamazi anazipereka kwa anthu antchito amene anazigwiritsa ntchito yokonzera nyumbayo. Koma sanawafunse kuti afotokoze kagwiritsidwe ntchito ka ndalama zolipira amene ankagwira ntchito, chifukwa anthuwo ankagwira ntchitoyo mokhulupirika kwambiri. Ndalama zomwe zinkaperekedwa pa nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yoperekedwa chifukwa cha tchimo sanabwere nazo ku Nyumba ya Yehova pakuti zinali za ansembe.
Pa nthawi imeneyo, Hazaeli, mfumu ya Aramu anapita kukathira nkhondo mzinda wa Gati nawulanda. Kenaka Hazaeli anatembenuka kupita kukathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Koma Yowasi mfumu ya Yuda anatenga zinthu zonse zopatulika zomwe anazipatula Yehosafati, Yehoramu, ndi Ahaziya abambo ake, mafumu a Yuda ndi mphatso zonse zomwe iye mwini anazipereka: golide yense amene anapezeka mʼnyumba yosungiramo chuma cha mʼnyumba ya Yehova ndi zomwe zinali mʼnyumba ya mfumu, nazipereka kwa Hazaeli mfumu ya Aramu. Pamenepo iye anachoka ku Yerusalemuko.
Ndipo ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Akuluakulu ake anamuchitira chiwembu ndi kumupha ku Beti Milo, pa njira yotsikira ku Silo. Yozakara mwana wa Simeati ndi Yehozabadi mwana wa Someri atumiki ake anamukantha nafa. Ndipo anamuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Amaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehowahazi Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi mwana wa Ahaziya mfumu ya Yuda, Yehowahazi, mwana wa Yehu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 17. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova potsatira machimo a Yeroboamu mwana Nebati amene anachimwitsa nawo Israeli ndipo iye sanawaleke machimowo. Ndipo Yehova anakwiyira Aisraeli nawayika pansi pa ulamuliro wa Hazaeli mfumu ya Siriya ndi Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli masiku awo onse.
Tsono Yehowahazi anapempha Yehova kuti amuchitire chifundo ndipo Yehova anamva pempho lake chifukwa anaona momwe mfumu ya Aramu inkapsinjira Aisraeli. Yehova anapatsa Aisraeli munthu woti awapulumutse ndipo anapulumuka mʼdzanja la Aramu. Choncho Aisraeli anakhala mʼnyumba zawo monga ankachitira kale. Komabe Aisraeli sanaleke kuchita machimo a nyumba ya Yeroboamu, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iwo anapitirira kuchita machimowo. Ndiponso fano la Asera linakhalabe ku Samariya.
Yehowahazi sanatsale ndi ankhondo ambiri koma 50 okha okwera pa akavalo, magaleta khumi ndi asilikali oyenda pansi 10,000.
Ntchito zina za Yehowahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Yehowahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya. Ndipo Yowasi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehowasi Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 37 cha Yowasi mfumu ya Yuda, Yehowahazi anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya, ndipo analamulira zaka 16. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanaleke kuchita tchimo la Yeroboamu mwana wa Nebati limene anachimwitsa nalo Israeli.
Ntchito zina za Yowasi ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Yowasi anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake ndipo Yeroboamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Yowasi anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli.
Tsono Elisa anadwala matenda amene anafa nawo. Yowasi mfumu ya Israeli inapita kukamuona ndipo inamulirira. Iye polira ankanena kuti, “Abambo anga! Abambo anga! Magaleta a Israeli ndi okwerapo ake a Israeli!”
Elisa anamuwuza kuti, “Tenga uta ndi mivi.” Ndipo anaterodi. Elisa anawuza mfumu ya Israeli kuti, “Tenga uta mʼdzanja lako.” Pamene anatenga utawo, Elisa anayika manja ake pa manja a mfumuyo.
Elisa anamuwuza kuti, “Tsekula zenera.” Ndipo anatsekuladi. Elisa anati, “Ponya muviwo!” Ndipo anaponyadi. Elisa anati, “Muvi wa chigonjetso cha Yehova, muvi wogonjetsera Aaramu! Iwe udzawawononga kwathunthu Aaramu ku Afeki.”
Kenaka Elisa anati, “Tenga mivi.” Ndipo mfumu inatenga miviyo. Iye anati, “Lasa pansi.” Mfumu inalasa pansi miviyo katatu nʼkuleka. Munthu wa Mulungu anapsera mtima mfumuyo ndipo anati, “Ukanalasa pansi kasanu kapena kasanu nʼkamodzi. Pamenepo ukanatha kuwagonjetsa Aaramu ndi kuwawononga kwathunthu. Koma tsopano udzawagonjetsa katatu kokha.”
Elisa anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda.
Tsono magulu a ankhondo a Amowabu ankabwera kudzalowa ndi kudzathira nkhondo dzikolo nthawi ya dzinja. Tsiku lina Aisraeli ena akukayika maliro mʼmanda, mwadzidzidzi anaona gulu lankhondo ndipo munthu womwalirayo anamuponyera mʼmanda a Elisa. Pamene mtembowo unakhudza mafupa a Elisa, munthu wakufayo anatsitsimuka nayimirira.
Hazaeli mfumu ya Aramu inazunza Aisraeli nthawi yonse ya ulamuliro wa Yehowahazi. Koma Yehova anawachitira chifundo Aisraeliwo ndi kukhudzika ndi zomwe zinkawachitikira chifukwa cha pangano lake ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo. Mpaka lero lino Iye sanafune kuwawononga kapena kuwachotsa pamaso pake.
Hazaeli mfumu ya Aramu inamwalira ndipo mwana wake Beni-Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Pamenepo Yowasi mwana wa Yehowahazi analandanso kwa Beni-Hadadi mwana wa Hazaeli mizinda yonse imene iye analanda Yehowahazi abambo ake. Yehowasi anagonjetsa Beni-Hadadi katatu ndipo anatenganso mizinda ya Israeli.
Amaziya Mfumu ya Yuda
Mʼchaka chachiwiri cha Yehowasi mwana wa Yowahazi mfumu ya Israeli, Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Iye anali ndi zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Yehoyadini wa ku Yerusalemu. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi zomwe anachita Davide kholo lake. Iye anatsatira zochita zonse za Yowasi abambo ake. Komabe sanachotse malo opembedzerapo mafano. Anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
Atakhazikika mu ufumu wake, Amaziya anapha atumiki ake amene anapha abambo ake, mfumu ija. Komatu iye sanaphe ana a anthu amene anapha abambo ake potsatira zomwe zinalembedwa mʼbuku la Malamulo a Mose. Mʼmenemo Yehova analamula kuti, “Makolo asaphedwe chifukwa cha ana awo, ndipo ana asaphedwe chifukwa cha makolo awo, koma aliyense ayenera kufa chifukwa cha zolakwa zake.”
Iye ndiye amene anapha Aedomu 10,000 mʼchigwa cha Mchere nalanda mzinda wa Sela pa nkhondo ndipo anawutcha Yokiteeli, dzina lake ndi lomwelo mpaka lero lino.
Tsono Amaziya anatuma amithenga kwa Yehowasi mwana wa Yehowahazi, mwana wa Yehu mfumu ya Israeli ndi kumuopseza kuti, “Bwera tidzaonane maso ndi maso.”
Koma Yehowasi mfumu ya Israeli anabweza mawu kwa Amaziya mfumu ya Yuda kuti, “Mtengo wa minga wa ku Lebanoni unatumiza uthenga kwa mkungudza wa ku Lebanoni. ‘Patse mwana wako wamkazi kuti ndimukwatire.’ Kenaka chirombo cha ku Lebanoni chinabwera ndi kupondaponda mtengo wa mingawo. Inde iwe wagonjetsa Edomu ndipo tsopano wayamba kudzikuza. Dzitamandire chifukwa cha kupambana kwako, koma khala kwanu konko! Nʼchifukwa chiyani ukuyamba dala mavuto amene adzakuwononga pamodzi ndi Yuda?”
Koma Amaziya sanamvere zimenezi. Choncho Yehowasi mfumu ya Israeli anakamuthira nkhondo. Yehowasi ndi Amaziya anakumana maso ndi maso ku Beti-Semesi mʼdziko la Yuda. Israeli anagonjetsa Yuda ndipo munthu aliyense anathawira kwawo. Yehowasi mfumu ya Israeli anagwira Amaziya mfumu ya Yuda, mwana wa Yowasi, mwana wa Ahaziya ku Beti-Semesi. Ndipo anapita ku Yerusalemu nakagwetsa khoma la Yerusalemu kuyambira ku Chipata cha Efereimu mpaka ku Chipata Chapangodya, gawo lotalika mamita 180. Iye anatenga golide ndi siliva yense pamodzi ndi ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndi zimene zinali mosungira chuma cha nyumba ya mfumu. Iye anagwiranso anthu nabwerera ku Samariya.
Ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene anachita, kuwonjezera za nkhondo yake ndi Amaziya mfumu ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Yehowasi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Samariya pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo mwana wake Yeroboamu analowa ufumu mʼmalo mwake.
Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda anakhala zaka khumi ndi zisanu atamwalira Yehowasi mwana wa Yehowahazi mfumu ya Israeli. Ntchito zina za Amaziya, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
Anthu anapangana zomuchita chiwembu mu Yerusalemu ndipo Amaziya anathawira ku Lakisi, koma anatumiza anthu ku Lakisiko nakamuphera komweko. Anabwera naye ku pa kavalo ku Yerusalemu ndi kumuyika mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide.
Ndipo anthu onse a ku Yuda anatenga Azariya, amene anali ndi zaka 16 namulonga ufumu mʼmalo mwa abambo ake Amaziya. Azariya anamanga mzinda wa Elati ndi kuwubwezeretsa ku Yuda, Amaziya atamwalira.
Mfumu Yeroboamu Wachiwiri wa ku Israeli
Mʼchaka cha khumi ndi chisanu cha Amaziya mwana wa Yowasi mfumu ya Yuda, Yeroboamu mwana wa Yehowasi mfumu ya Israeli analowa ufumu ku Samariya ndipo analamulira za 41. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli. Iye ndi amene anabwezeretsanso malire a Israeli kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Nyanja ya Araba, molingana ndi zimene ananena Yehova Mulungu wa Israeli, kudzera mwa mtumiki wake Yona mwana wa Amitai, mneneri wochokera ku Gati-Heferi.
Pakuti Yehova anaona masautso a Israeli amene anali owawa kwambiri, panalibe kapolo kapena mfulu ngakhale wina aliyense amene akanathandiza Israeli. Pakuti Yehova anali asananene zofafaniza ufumu wa Israeli pa dziko lapansi, Iye anawapulumutsa kudzera mʼdzanja la Yeroboamu mwana wa Yowasi.
Ntchito zina za Yeroboamu ndi zonse zimene anachita, za kupambana kwake pa nkhondo, za mmene anagonjetsera Damasiko ndi Hamati, imene inali mizinda ya Yuda, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Yeroboamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi mafumu a Israeli. Ndipo Zekariya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Azariya Mfumu ya Yuda
Mʼchaka cha 27 cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Azariya mwana wa Amaziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 16 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali Yekoliya wa ku Yerusalemu. Iyeyo anachita zabwino pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Amaziya abambo ake. Komabe malo opembedzerako mafano sanawachotse ndipo anthu anapitirizabe kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
Ndipo Yehova analanga mfumu ndi nthenda ya khate mpaka tsiku limene inamwalira. Tsono mfumuyo inkakhala mʼnyumba yakeyake yapadera. Mwana wake Yotamu ndiye amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu ndiponso ndiye amene ankalamulira anthu mʼdzikomo.
Ntchito zina za Azariya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Azariya anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Yotamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Zekariya Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 38 cha Azariya mfumu ya Yuda, Zekariya mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira makolo ake. Iye sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
Salumu mwana wa Yabesi anachitira chiwembu Zekariya. Anamukantha anthu akuona, namupha, ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake. Ntchito zina za Zekariya, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. Awa ndiwo mawu a Yehova amene anayankhula kwa Yehu kuti, “Ana ako adzalamulira Israeli mpaka mʼbado wachinayi.”
Salumu Mfumu ya Israeli
Salumu mwana wa Yabesi anakhala mfumu mʼchaka cha 39 cha ulamuliro wa Uziya mfumu ya Yuda ndipo analamulira mu Samariya mwezi umodzi. Ndipo Menahemu mwana wa Gadi anachoka ku Tiriza napita ku Samariya nakantha Salumu mwana wa Yabesi ku Samariya, namupha ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ntchito zina za Salumu ndiponso za chiwembu chimene anachita, zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
Nthawi imeneyo Menahemu, kuchokera ku Tiriza, anakathira nkhondo mzinda wa Tipisa ndi anthu onse amene anali mʼmenemo ndi dera lonse lozungulira chifukwa iwo anakana kutsekula zipata zawo. Iye anatenga katundu yense mu mzinda wa Tipisa ndi kutumbula akazi onse oyembekezera.
Menahemu Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 39 cha Azariya mfumu ya Yuda, Menahemu mwana wa Gadi anakhala mfumu ya Israeli ndipo analamulira mu Samariya zaka khumi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Nthawi yonse ya ulamuliro wake sanasiye machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
Tsono Puli mfumu ya ku Asiriya inadzathira nkhondo dzikolo ndipo Menahemu anapatsa Puliyo makilogalamu 34,000 a siliva kuti amuthandize ndi kulimbikitsa ufumu wake. Menahemu anapeza ndalamazo kudzera mu msonkho umene ankakhometsa Aisraeli. Munthu aliyense wachuma ankapereka masekeli a siliva makumi asanu kwa mfumu ya ku Asiriya. Choncho mfumu ya ku Asiriya inabwerera ndipo sinakhalenso mʼdzikomo.
Ntchito zina za Menahemu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Menahemu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Pekahiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Pekahiya Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha makumi asanu a Azariya mfumu ya Yuda, Pekahiya mwana wa Menahemu anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka ziwiri. Pekahiya anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Iye sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, omwe anachimwitsa nawo Israeli. Ndipo Peka mwana wa Remaliya, mtsogoleri wake wa ankhondo, anamuchita chiwembu. Iye pamodzi ndi anthu makumi asanu a ku Giliyadi anapha Pekahiya pamodzi ndi Arigobu ndi Ariyeli mʼchipinda choteteza nyumba ya mfumu mu Samariya. Kotero Peka anapha Pekahiya ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ntchito zina za Pekahiya ndi zonse zimene anachita zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli.
Peka Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 52 cha Azariya mfumu ya Yuda, Peka mwana wa Remaliya anakhala mfumu ya Israeli ku Samariya ndipo analamulira zaka makumi awiri. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanaleke machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa nawo Israeli.
Nthawi ya Peka mfumu ya Israeli, Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera ndi kudzalanda Iyoni, Abeli-Beti-Maaka, Yanowa, Kedesi ndi Hazori. Mfumu ya ku Asiriya inatenga Giliyadi ndi Galileya, kuphatikizanso madera onse a Nafutali ndipo anatumiza Aisraeli ku Asiriya. Kenaka Hoseya mwana wa Ela anachitira chiwembu Peka mwana wa Remaliya. Anamukantha ndi kumupha ndipo anakhala mfumu mʼmalo mwake mʼchaka makumi awiri cha Yotamu mwana wa Uziya.
Ntchito zina za Peka ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
Yotamu Mfumu ya Yuda
Mʼchaka chachiwiri cha Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli, Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Iye anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Amayi ake anali Yerusa mwana wa Zadoki. Iye anachita zabwino pamaso pa Yehova monga anachitira Uziya abambo ake. Komabe malo opembedzera mafano sanawachotse ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko.
Ntchito zina za Yotamu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? (Nthawi imeneyo, Yehova anayamba kumatuma Rezini mfumu ya Aaramu ndi Peka mwana wa Remaliya kudzamenyana ndi Yuda). Yotamu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Ahazi mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ahazi Mfumu ya Yuda
Mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya, Ahazi mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anayamba kulamulira. Ahazi anakhala mfumu ali ndi zaka makumi awiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 16. Iye sanachite zabwino pamaso pa Yehova Mulungu wake monga momwe Davide kholo lake ankachitira. Iye anayenda mʼnjira ya mafumu a Israeli mpaka kupereka mwana wake wamwamuna pa moto ngati nsembe yopsereza, potsatira zonyansa za anthu a mitundu imene Yehova anayipirikitsa mʼdzikomo Aisraeli asanafike. Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzera mafano, pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri.
Ndipo Rezini mfumu ya Aramu ndi Peka mwana wa Remaliya mfumu ya Israeli anapita kukachita naye nkhondo ku Yerusalemu ndipo anazinga Ahazi, koma sanathe kumugonjetsa. Nthawi imeneyo Rezini mfumu ya Aramu anatenganso Elati ndi kumubwezera kwa Aaramu, nathamangitsa anthu a ku Yuda mu Elatimo. Aedomu anapita kukakhala ku Elati ndipo akukhalako mpaka lero lino.
Ahazi anatuma amithenga kwa Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya kuti, “Ine ndine mtumiki wanu ndipo ndili pansi panu. Bwerani mudzandipulumutse mʼdzanja la mfumu ya Aramu ndiponso mʼdzanja la mfumu ya Israeli amene akundithira nkhondo.” Ndipo Ahazi anatenga siliva ndi golide amene anamupeza mʼNyumba ya Yehova ndi mosungira chuma cha nyumba ya mfumu ndi kutumiza ngati mphatso kwa mfumu ya ku Asiriya. Mfumu ya ku Asiriya inamvera pokathira nkhondo mzinda wa Damasiko ndi kuwulanda. Anthu a mu mzindamo anawatumiza ku Kiri ndipo anapha Rezini.
Kenaka mfumu Ahazi inapita ku Damasiko kukakumana ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya. Iye anaona guwa lansembe ku Damasiko kuja ndipo anatumiza chitsanzo chake kwa wansembe Uriya, osasiyapo nʼkanthu komwe kuti athe kulimanga. Choncho wansembe Uriya anamanga guwa lansembe molingana ndi chitsanzo chimene anamutumizira Mfumu Ahazi kuchokera ku Damasiko ndipo anatsiriza kumanga guwalo Ahazi asabwere kuchokera ku Damasiko kuja. Mfumu itabwera kuchokera ku Damasiko kuja ndi kuona guwalo, inasendera pafupi ndi kupereka nsembe paguwapo. Mfumu inapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya chakudya. Inapereka nsembe yachakumwa ndi kuwaza magazi a nsembe yake yachiyanjano paguwapo. Guwa lamkuwa limene linali pamaso pa Yehova analichotsa kutsogolo kwa nyumbayo, kulichotsa pakati pa guwa latsopano ndi Nyumba ya Yehova ndi kukaliyika cha kumpoto kwa guwa latsopanolo.
Pamenepo Mfumu Ahazi inalamula wansembe Uriya kuti, “Pa guwa lalikulu latsopano uziperekapo nsembe yopsereza ya mmawa ndi nsembe ya chakudya ya madzulo, nsembe yopsereza ya mfumu ndi nsembe yake ya chakudya ndiponso nsembe za anthu onse a mʼdziko, za chakudya ndi chakumwa. Pa guwali uziwazapo magazi a nsembe zonse zopsereza ndi nsembe zina zonse. Koma ine ndizigwiritsa ntchito guwa lansembe lamkuwa pofuna kufunsira nzeru.” Ndipo wansembe Uriya anachita monga analamulira Mfumu Ahazi.
Mfumu Ahazi anachotsa maferemu a maphaka nachotsapo mabeseni. Iye anatsitsa mbiya yayikulu imene inali pamwamba pa ngʼombe zamkuwa ndipo anayika pansi pa chiwundo cha miyala. Iye anachotsa kadenga ka pa Sabata kamene kanamangidwa mʼkati mwa Nyumba ya Yehova ndiponso anatseka chipata cholowera mfumu cha kunja kwa nyumba ya Yehova pofuna kukondweretsa mfumu ya ku Asiriya.
Ntchito zina za Ahazi ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Hoseya Mfumu Yotsiriza ya Israeli
Mʼchaka cha 12 cha Ahazi mfumu ya Yuda, Hoseya mwana wa Ela anakhala mfumu ya Israeli mu Samariya ndipo analamulira zaka zisanu ndi zinayi. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, koma osafanana ndi mafumu a Israeli amene ankalamulira iye asanalowe ufumuwo.
Salimenezeri mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo Hoseya amene anali pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iyeyo. Koma mfumu ya ku Asiriya inazindikira kuti Hoseya akuwukira, pakuti Hoseyayo anali atatumiza nthumwi kwa So mfumu ya Igupto ndiponso analeka kukhoma msonkho kwa mfumu ya ku Asiriya, monga ankachitira chaka ndi chaka. Choncho Salimenezeri anagwira Hoseya ndi kumuyika mʼndende. Mfumu ya ku Asiriya inapita kukathira nkhondo dziko lonse la Israeli ndipo inapita mpaka ku Samariya ndipo inazinga mzindawo kwa zaka zitatu. Mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya, mfumu ya ku Asiriya inalanda Samariya ndipo inatenga Aisraeli ndi kupita nawo ku Asiriya. Anakawakhazika ku Hala ndi Habori mʼmbali mwa mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi.
Israeli Apita ku Ukapolo chifukwa cha Tchimo
Zonsezi zinachitika chifukwa Aisraeli anachimwira Yehova Mulungu wawo, amene anawatulutsa mʼdziko la Igupto pansi pa ulamuliro wa Farao mfumu ya Igupto. Iwo ankapembedza milungu ina, ndiponso ankatsatira miyambo ya anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika mʼdzikomo pamodzinso ndi miyambo yonse imene mafumu a Israeli anayambitsa. Ndipo Aisraeli ankachita zoyipa mwamseri kutsutsana ndi Yehova Mulungu wawo. Kuchokera ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa, mʼmizinda yawo yonse anamangamo malo opembedzeramo mafano. Anayimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya mafano a Asera pa phiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. Pa malo aliwonse opembedzera mafano, anthuwa ankafukiza lubani monga momwe ankachitira anthu a mitundu imene Yehova anayichotsa pamene iwo ankafika. Iwo anachita zinthu zoyipa zomwe zinaputa mkwiyo wa Yehova. Ndipo iwowo ankapembedza mafano ngakhale Yehova ananena kuti, “Musadzachite zimenezi.” Yehova anachenjeza Israeli ndi Yuda kudzera mwa aneneri ake onse ndi alosi kuti, “Lekani mchitidwe wanu woyipawo. Mverani malamulo anga ndi malangizo anga potsatira zonse zolembedwa mʼmalamulo a Mose, zimene ndinalamulira makolo anu kuti azimvere, kudzera mwa aneneri, atumiki anga.”
Koma anthuwa sanamvere ndipo anawumitsa khosi ngati momwe analili makolo awo, amene sanadalire Yehova Mulungu wawo. Anakana malangizo ake ndi pangano anachita ndi makolo awo ndipo ananyoza zochenjeza za Yehova. Iwo anatsatira mafano achabechabe nasanduka achabechabe. Anthuwa anatsanzira mitundu ya anthu owazungulira ngakhale kuti Yehova anawalamula kuti, “Musamachite zomwe iwo amachita,” koma iwo anachita zomwe Yehova anawaletsa.
Iwowo anasiya malamulo onse a Yehova Mulungu wawo, nadzipangira mafano awiri osungunula a ana angʼombe ndiponso fano la Asera, napembedza zonse zamlengalenga ndi kutumikira Baala. Ndipo anadutsitsa mʼmoto ana awo aamuna ndi aakazi. Iwo ankawombeza mawula, namachitanso zanyanga ndipo anadzipereka kuchita zoyipa pamaso pa Yehova namukwiyitsa.
Choncho Yehova anakwiya nawo kwambiri Aisraeli ndipo anawachotsa pamaso pake. Palibe amene anatsala kupatula fuko la Yuda lokha. Yuda nayenso sanasunge malamulo a Yehova Mulungu wawo. Iwo ankatsatira machitidwe amene Israeli anayambitsa. Motero Yehova anakana Aisraeli onse. Iye anawazunza nawapereka mʼmanja mwa anthu ofunkha mpaka Iye atawachotseratu pamaso pake.
Yehova atangʼamba Israeli kumuchotsa ku nyumba ya Davide, Aisraeliwo anasankha Yeroboamu mwana wa Nebati kukhala mfumu yawo. Yeroboamu ananyengerera Aisraeli kuti asatsatire Yehova ndipo anawachimwitsa tchimo lalikulu. Aisraeli anakakamira machimo onse amene Yeroboamu anachita ndipo sanawasiye mpaka pamene Yehova anawachotsa pamaso pake monga anawachenjezera kudzera mwa atumiki ake onse, aneneri. Choncho Aisraeli anachotsedwa mʼdziko lawo kupita ku ukapolo ku Asiriya ndipo ali komweko mpaka lero lino.
Anthu Achilendo Akhala mu Samariya
Mfumu ya ku Asiriya inabweretsa anthu a ku Babuloni, Kuta, Awa, Hamati ndi a ku Sefaravaimu kudzawakhazika mʼmizinda ya Samariya kulowa mʼmalo mwa Aisraeli. Iwo anatenga Samariya ndi kukhala mʼmizinda yake. Iwo atayamba kukhala kumeneko, sanapembedze Yehova choncho Yehova anatumiza mikango pakati pawo ndipo inapha ena mwa iwo. Tsono mfumu ya ku Asiriya inawuzidwa za nkhaniyi kuti, “Anthu amene munawatumiza ndi kuwakhazika mʼmizinda ya Samariya sakudziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna. Choncho Iye watumiza mikango pakati pawo imene ikuwapha chifukwa anthuwo sadziwa chimene Mulungu wa dzikolo amafuna.”
Tsono mfumu ya ku Asiriya inalamula kuti, “Tengani wansembe mmodzi mwa amene munawagwira ukapolo, mupite naye kumeneko ndipo akakhale komweko nakaphunzitse anthu zimene Mulungu wa dzikolo amafuna.” Choncho mmodzi mwa ansembe amene anawatenga ku Samariya anabwera kudzakhala ku Beteli ndipo ankaphunzitsa anthuwo kupembedza Yehova.
Koma mtundu uliwonse wa anthu unkapangabe mafano a milungu yawoyawo mʼmizinda yambiri imene anthuwo ankakhala, ndipo anayika milunguyo mʼnyumba za milungu zimene anthu a ku Samariya anamanga ku malo opembedzera mafano. Anthu a ku Babuloni anapanga Sukoti-Benoti, anthu a ku Kuti anapanga Nerigali, ndipo anthu a ku Hamati anapanga Asima; Aava anapanga Nibihazi ndi Taritaki, ndipo Asefaravaimu ankawotcha ana awo pa moto ngati nsembe kwa Adirameleki ndi Anameleki, milungu ya Asefaravaimu. Iwo ankapembedza Yehova, koma ankadzisankhira okha pakati pawo anthu wamba kuti akhale ansembe awo ku nyumba za milungu za ku malo opembedzera mafano. Iwowo ankapembedza Yehova, komanso ankatumikira milungu yawo molingana ndi miyambo ya mitundu ya kumene ankachokera.
Mpaka lero lino iwo akupitirizabe kuchita zimene ankachita poyamba. Sapembedza Yehova kapenanso kutsata malangizo ake ndi malamulo ake, chiphunzitso chake monga mwa malamulo amene Yehova anawapereka kwa zidzukulu za Yakobo, amene anamutcha Israeli. Pamene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli, Iye anawalamula kuti, “Musapembedze milungu ina kapena kuyigwadira iyo, kuyitumikira kapena kupereka nsembe kwa iyoyo. Koma Yehova amene anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu ndiye amene muyenera kumupembedza. Muyenera kusamalitsa nthawi zonse kusunga malangizo anga ndi malemba anga, chiphunzitso ndi malamulo amene anakulemberani. Musapembedze milungu ina. Musayiwale pangano limene ndinapangana nanu ndipo musamapembedze milungu ina. Mʼmalo mwake muzipembedza Yehova Mulungu wanu pakuti ndiye amene adzakulanditsani mʼdzanja la adani anu onse.”
Komabe iwo sanamvere ndipo anapitiriza kuchita zomwe ankachita kale. Ngakhale anthuwo ankapembedza Yehova, ankatumikiranso mafano awo. Mpaka lero lino ana awo ndi zidzukulu zawo zikupitiriza kuchita zomwe ankachita makolo awo.
Hezekiya Mfumu ya Yuda
Mʼchaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu. Anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Abi, mwana wa Zekariya. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. Anachotsa malo opembedzerako mafano, anaphwanya miyala yachipembedzo ndiponso anadula mafano a Asera. Iye anaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, pakuti mpaka kufikira nthawi imeneyi Aisraeli amafukiza lubani kwa njoka imeneyi. (Imatchedwa Nehusitani).
Hezekiya anadalira Yehova Mulungu wa Israeli. Kotero panalibe wina wofanana naye pakati pa mafumu onse a Yuda, asanakhale mfumu kapena atakhala kale mfumu. Iye anakangamira Yehova ndipo sanamusiye koma anasunga malamulo amene Yehova anapatsa Mose. Ndipo Yehova anali naye ndipo kulikonse kumene anapita zinthu zinkamuyendera bwino. Iye anagalukira mfumu ya ku Asiriya ndipo sanayitumikirenso. Iye anakantha Afilisti kuyambira ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa. Anakafika mpaka ku Gaza ndi ku malire ake.
Mʼchaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Salimenezeri, mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya ndi kuwuzinga Asiriya analanda mzindawu patatha zaka zitatu. Choncho mzinda wa Samariya unalandidwa chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya mfumu ya Israeli. Mfumu ya ku Asiriya inatenga Aisraeli kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya ndipo anakawakhazika ku Hala, ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi. Izi zinachitika chifukwa sanamvere zonena za Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula. Iwo sanamvere malamulowo kapena kuwagwiritsa ntchito.
Mʼchaka chakhumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, nayilanda. Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya ku Asiriya ku Lakisi wonena kuti, “Ine ndalakwa. Chokani kuno ndipo ndidzakupatsani chilichonse chimene munene.” Mfumu ya ku Asiriya inalamula mfumu Hezekiya, mfumu ya Yuda, kuti azipereka makilogalamu a siliva okwana 3,000 ndi makilogalamu a golide 1,000. Mfumu Hezekiya inapereka siliva yense amene anapezeka mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba zosungiramo chuma cha mfumu.
Nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anakanganula golide amene anakuta zitseko ndi mphuthu za chipata cha Nyumba ya Yehova namupereka kwa mfumu ya ku Asiriya.
Senakeribu Aopseza Yerusalemu
Mfumu ya ku Asiriya inatuma Taritani, Rabusarisi ndi Rabusake pamodzi ndi gulu lalikulu la ankhondo, kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwo anafika ku Yerusalemu nakayima pafupi ndi ngalande ya madzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu waukulu wopita ku malo a Munda wa Mmisiri Wochapa. Iwo anayitana mfumu, ndipo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa anthuwo.
Ndipo Rabusake anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,
“ ‘Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, ‘Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?’ Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.’ ” Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, “Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa lansembe ili mu Yerusalemu?”
“ ‘Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! Ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo? Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga malo ano popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.’ ”
Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina ndi Yowa anawuza Rabusakeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
Koma Rabusake anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
Tsono Rabusake anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! Zimene mfumu ikunena ndi izi: ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni mʼdzanja langa. Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
“Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, mpaka nditabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanuli, dziko la tirigu ndi vinyo watsopano, dziko la chakudya ndi minda ya mipesa, dziko la mitengo ya olivi ndi uchi. Sankhani moyo osati imfa!
“Musamvere zonena Hezekiya, pakuti iye akukusocheretsani ponena kuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ Kodi mulungu wa anthu a mtundu wina uliwonse wapulumutsapo dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, Hena ndi Ivani? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja langa? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”
Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu, mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza Hezekiya zonse zimene anayankhula Rabusake uja.
Kupulumutsidwa kwa Yerusalemu
Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”
Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.
“Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”
Yankho la Mulungu Kudzera mwa Yesaya
Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:
“Namwali wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka iwe.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu
akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.
Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?
Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako
ndi kumuyangʼana monyada?
Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!
Kudzera mwa amithenga ako
wonyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta ochuluka
ndinakwera mapiri ataliatali,
pa msonga za mapiri a Lebanoni.
Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,
mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.
Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,
mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndipo ndinamwa madzi a kumeneko.
Ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ”
“ ‘Kodi sunamvepo?
Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndachita kuti zichitikedi,
iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,
athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.
Ali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu womera pa denga,
umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”
“ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,
kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
ndi mkwiyo wako pa Ine.
Chifukwa chakuti wandikwiyira
ndipo ndamva za mwano wako,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa
njira yomwe unadzera pobwera.’
“Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:
“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,
ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.
Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,
mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale
adzazika mizu ndi kubereka zipatso.
Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”
“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
“Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:
“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi.
Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake
kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,
akutero Yehova.
Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.
Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
Kudwala kwa Hezekiya
Masiku amenewo Hezekiya anadwala ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi anapita kukamuona ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti: Konza nyumba yako chifukwa umwalira ndipo suchira.”
Hezekiya anatembenuka nayangʼana ku khoma ndipo anapemphera kwa Yehova kuti, “Inu Yehova, kumbukirani ndithu mmene ndayendera mokhulupirika ndi mtima wonse ndipo ndachita zolungama pamaso panu.” Hezekiya analira kwambiri.
Yesaya asanatuluke mʼbwalo lapakati, Yehova anayankhula kuti, “Bwerera, kamuwuze Hezekiya mtsogoleri wa anthu anga kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako akuti: Ndamva pemphero lako ndipo misozi yako ndayiona ndipo ndidzakuchiritsa. Tsiku lachitatu kuchokera lero udzapita ku Nyumba ya Yehova. Ndidzawonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzinda umenewu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya. Ndidzateteza mzinda umenewu chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
Pamenepo Yesaya anati, “Konzani phala lankhuyu.” Iwo anakonza phalalo nalipaka pa chithupsacho ndipo Hezekiya anachira.
Tsono Hezekiya anafunsa Yesaya kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Yehova adzandichiritsa ndi kuti ndidzapita ku Nyumba ya Yehova pa tsiku lachitatu kuchokera lero lino?”
Yesaya anayankha kuti, “Chizindikiro cha Yehova chosonyeza kuti Iye adzachita chimene walonjeza ndi ichi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?”
Hezekiya anati, “Nʼchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, kulekana nʼkuti chithunzithunzicho chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi.”
Pamenepo mneneri Yesaya anapemphera kwa Yehova ndipo Yehova anachititsa kuti chithunzithunzi chibwerere mʼmbuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi anamanga.
Akazembe Ochokera ku Babuloni
Pa nthawi imeneyo Merodaki-Baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babuloni anatumiza amithenga kwa Hezekiya kukapereka makalata ndi mphatso, chifukwa nʼkuti atamva za kudwala kwa Hezekiyayo. Hezekiya analandira amithengawo ndipo anawaonetsa zonse zimene zinali mʼnyumba zake zosungiramo chuma. Anawaonetsa siliva, golide, zonunkhiritsa zakudya ndi mafuta abwino kwambiri, zida zake zankhondo ndiponso china chilichonse chimene chinali mosungiramo zinthu zake. Panalibe chinthu mʼnyumba yake yaufumu kapena mu ufumu wake wonse chimene Hezekiya sanawaonetse.
Tsono mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya namufunsa kuti, “Kodi anthu aja anakuwuzani zotani ndipo anachokera kuti?”
Hezekiya anayankha kuti, “Anachokera ku dziko lakutali, ku Babuloni.”
Mneneriyo anafunsa kuti, “Kodi anaona chiyani mʼnyumba yanu yaufumu?”
Hezekiya anayankha kuti, “Anaona china chilichonse mʼnyumba yanga yaufumu ndipo palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindinawaonetse mʼnyumba zanga zosungiramo chuma.”
Pamenepo Yesaya anawuza Hezekiya kuti, “Imvani zimene Yehova akunena: Taonani, masiku akubwera ndithu pamene zonse za mʼnyumba yanu yaufumu, zonse zimene makolo anu anazisunga mpaka lero, zidzatengedwa kupita ku Babuloni. Palibe chimene chidzatsale, akutero Yehova. Ndipo ena mwa ana anu omwe, amene mudzabereke adzatengedwa ndipo adzawasandutsa anthu ofulidwa mʼnyumba yaufumu ya mfumu ya Babuloni.”
Hezekiya anayankha kuti, “Mawu a Yehova amene mwayankhulawa ndi abwino. Pakuti iye ankaganiza kuti, ‘Kodi pa nthawi yanga sipadzakhala mtendere ndi bata?’ ”
Ntchito zina za Hezekiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Hezekiya anamwalira nagona pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Manase mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Manase Mfumu ya Yuda
Manase anakhala mfumu ali ndi zaka khumi ndi ziwiri ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 55. Amayi ake anali Hefiziba. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, potsatira mchitidwe wonyansa wa mitundu imene Yehova anayipirikitsa pofika Aisraeli. Iyetu anamanganso malo opembedzera mafano amene Hezekiya abambo ake anawawononga. Anamangira Baala maguwa a nsembe ndi mtengo wa fano la Asera monga anachitira Ahabu mfumu ya Israeli ndipo ankapembedza zolengedwa zonse zamlengalenga. Anamanga maguwa ansembewa mʼNyumba ya Yehova, mʼmene Yehova ananena kuti, “Mu Yerusalemu ndidzayikamo Dzina langa.” Mʼmabwalo onse awiri a Nyumba ya Yehova, Manase anamangamo maguwa opembedzerapo zinthu zamlengalenga. Iye anapsereza mwana wake pa moto ngati nsembe, ankachita za matsenga, ankawombeza mawula, ankapita kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ndiponso ankapembedza mizimu. Iyeyo anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova ndipo anakwiyitsa Yehovayo.
Iye anatenga fano losema la Asera limene analipanga ndi kuliyika mʼNyumba ya Yehova, Nyumba imene Yehova ananena kwa Davide ndi mwana wake Solomoni kuti, “Mʼnyumba iyi ndi mu Yerusalemu ndiwo malo amene ndasankha pakati pa mafuko onse a Aisraeli kuyikamo Dzina langa kwamuyaya. Sindidzalola kuti Aisraeli achotsedwe mʼdziko lawo limene ndinapatsa makolo awo ngati iwowo adzasamala kuchita zinthu zonse zimene ndinawalamula ndi kusunga malamulo onse amene mtumiki wanga Mose anawapatsa.” Koma anthu sanamvere. Manase anawasocheretsa, kotero kuti anachita zoyipa zambiri kupambana anthu a mitundu ina amene Yehova anawawononga pamene Aisraeli ankafika.
Yehova anayankhula kudzera mwa atumiki ake, aneneri kuti, “Manase mfumu ya Yuda wachita machimo onyansawa ndipo wachita zoyipa kupambana Aamori amene analipo kale iye asanabadwe ndi kuchimwitsa anthu a ku Yuda ndi mafano ake. Choncho Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taonani, ndikubweretsa pa Yerusalemu ndi Yuda mavuto akuti aliyense amene adzawamve adzathedwa nzeru. Ndidzalanga Yerusalemu ndi Yuda pogwiritsa ntchito muyeso umene ndinalangira Samariya ndi Ahabu pamodzi ndi nyumba yake. Ndidzayeretsa Yerusalemu monga mmene munthu amachitira popukuta mbale ndipo atayipukuta amayivundikira pansi. Ndidzawataya anthu otsala amene ndi cholowa changa ndipo ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo. Adzachotsedwa ndipo adaniwo adzawalanda zinthu zonse chifukwa anachita zoyipa pamaso panga ndipo akhala akundikwiyitsa kuchokera tsiku limene makolo awo anatuluka mu Igupto mpaka lero lino.’ ”
Kuwonjezera apo, Manase anakhetsa kwambiri magazi a anthu osalakwa mpaka magaziwo kuyenderera mu Yerusalemu kuyambira mbali ina mpaka mbali ina, kuphatikiza pa kuchimwitsa Yuda, kotero kuti anthu anachita zoyipa pamaso pa Yehova.
Ntchito zina za Manase ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Manase anagona ndi makolo ake ndipo anayikidwa mʼmanda mʼmunda wa Uza, ku nyumba yaufumu. Ndipo Amoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Amoni Mfumu ya Yuda
Amoni anakhala mfumu ali ndi zaka 22 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka ziwiri. Amayi ake anali Mesulemeti mwana wa Haruzi, wochokera ku Yotiba. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Manase abambo ake. Anatsatira makhalidwe onse a abambo ake. Ankapembedza mafano amene abambo akewo ankawapembedza ndipo ankawagwadira. Iyeyo anasiya Yehova Mulungu wa makolo ake ndipo sanayende mʼnjira ya Yehova.
Nduna za Amoni zinamuchita chiwembu ndipo zinamupha mʼnyumba yake. Koma anthu a mʼdzikomo anapha onse amene anachitira chiwembu Mfumu Amoni, nayika Yosiya mwana wake kukhala mfumu mʼmalo mwake.
Ntchito zina za Amoni ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Iye anayikidwa mʼmanda ake mʼmunda wa Uza. Ndipo Yosiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Buku la Malamulo Lipezeka
Yosiya anakhala mfumu ali ndi zaka zisanu ndi zitatu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 31. Amayi ake anali Yedida mwana wa Adaiya wochokera ku Bozikati. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo anayenda mʼnjira zonse za Davide kholo lake, osatembenukira kumanja kapena kumanzere.
Mʼchaka cha 18 cha ufumu wake, Mfumu Yosiya anatuma mlembi wa nyumba ya mfumu, Safani, mwana wa Azariya, mwana wa Mesulamu, ku Nyumba ya Yehova. Iye anati, “Pita kwa mkulu wa ansembe Hilikiya ndipo ukamuwuze kuti awerenge ndalama zimene anthu abwera nazo ku Nyumba ya Yehova, zimene alonda a pa khomo anasonkhanitsa kwa anthu. Ndalamazo azipereke kwa anthu amene asankhidwa kuti ayangʼanire ntchito ya Nyumba ya Yehova. Ndipo anthu amenewa azilipira antchito amene akukonzanso Nyumba ya Yehova, amisiri a matabwa, amisiri omanga ndi amisiri a miyala. Iwo akagulenso matabwa ndi miyala yosemedwa kuti akonzere Nyumba ya Yehova. Koma anthu amene apatsidwa ndalama zolipira antchito okonza Nyumbayo asawafunse za kagwiritsidwe ntchito ka ndalamazo, popeza ndi anthu wokhulupirika.”
Mkulu wa ansembe Hilikiya anawuza Safani, mlembiyo kuti, “Ndapeza Buku la Malamulo mʼNyumba ya Yehova.” Anapereka bukulo kwa Safani amene analiwerenga. Ndipo Safani mlembi uja, anapita nakafotokozera mfumu kuti, “Atumiki anu apereka ndalama zija zinali mʼNyumba ya Yehova kwa anthu amene akugwira ntchito ndi kuyangʼanira ntchito yokonza Nyumba ya Yehova.” Kenaka Safani mlembiyo, anafotokozera mfumu kuti, “Wansembe Hilikiya wandipatsa buku.” Ndipo Safani analiwerenga pamaso pa mfumu.
Mfumu itamva mawu a mʼBuku la Malamulo, inangʼamba zovala zake. Iyo inalamula wansembe Hilikiya, Ahikamu mwana wa Safani, Akibo mwana wa Mikaya, Safani mlembi uja ndi Asaiya mtumiki wa mfumu, kuti, “Pitani mukafunse Yehova mʼmalo mwanga ndi mʼmalo mwa anthu onse a mʼdziko la Yuda, za zomwe zalembedwa mʼbuku limene lapezekali. Mkwiyo wa Yehova ndi waukulu kwambiri pa ife ndipo watiyakira chifukwa makolo athu sanamvere mawu a buku ili. Iwo sanachite molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼmenemu zokhudza ife.”
Choncho Hilikiya wansembe, Ahikamu, Akibo, Safani ndi Asaiya anapita kukayankhula ndi Hulida, mneneri wamkazi, mkazi wa Salumu mwana wa Tikiva, mwana wa Harihasi, wosunga zovala zaufumu. Mneneri wamkaziyu ankakhala mu Yerusalemu, ku chigawo chachiwiri cha mzindawo.
Ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti: Kamuwuzeni munthu amene wakutumani kwa ine kuti, ‘Ichi ndi chimene Yehova akunena: Taonani, ndidzabweretsa mavuto pa malo ano ndi pa anthu ake, molingana ndi zonse zimene zalembedwa mʼbuku limene mfumu ya Yuda yawerenga. Chifukwa anthuwo andisiya Ine ndi kumafukiza lubani kwa milungu ina nandikwiyitsa ndi mafano onse amene manja awo anapanga, mkwiyo wanga udzayaka pa malo ano ndipo sudzazimitsidwa.’ Koma mfumu ya Yuda imene inakutumani kuti mudzafunse kwa Yehova kayiwuzeni kuti, ‘Ichi ndi chimene Yehova Mulungu wa Israeli akunena molingana ndi mawu amene unamva: Chifukwa unasweka mtima ndi kudzichepetsa wekha pamaso pa Yehova, pamene unamva zomwe zinayankhulidwa zotsutsana ndi malo ano ndi anthu ake, kuti adzakhala otembereredwa nasanduka bwinja, ndiponso chifukwa unangʼamba zovala ndi kulira pamaso panga, ndamva pemphero lako, akutero Yehova. Choncho taona, Ine ndidzakutenga kupita kwa makolo ako ndipo udzayikidwa mʼmanda mwako mwamtendere. Maso ako sadzaona mavuto onse amene ndidzabweretse pamalo pano.’ ”
Ndipo anthu aja anabwerera nakafotokoza mawu amenewa kwa mfumu.
Yosiya Akonzanso Pangano
Pamenepo mfumu inayitanitsa akuluakulu onse a ku Yuda ndi Yerusalemu. Mfumuyo inapita ku Nyumba ya Yehova pamodzi ndi anthu onse a ku Yuda, ndi onse okhala mu Yerusalemu, ansembe ndi aneneri, ndiponso anthu ena onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. Mfumuyo inawerenga mawu onse a mʼBuku la Chipangano limene linapezeka mʼNyumba ya Yehova, anthu onse akumva. Mfumu inayimirira pambali pa chipilala ndi kuchita pangano pamaso pa Yehova kuti idzatsatira Yehova ndi kusunga malamulo, mawu ndi malangizo ake ndi mtima wonse ndi moyo wonse, kukwaniritsa mawu a mʼpanganoli, olembedwa mʼbukuli. Pamenepo anthu onse anadzipereka kutsatira panganoli.
Mfumu inalamula wansembe wamkulu Hilikiya, ansembe othandizana naye ndi alonda a pa khomo kuti achotse mʼNyumba ya Yehova ziwiya zonse zopembedzera Baala ndi Asera ndiponso mafano a zinthu zamlengalenga. Yosiya anazitentha kunja kwa Yerusalemu, ku minda ya ku Chigwa cha Kidroni ndipo phulusa lake anapita nalo ku Beteli. Iye anachotsa ansembe a mafano amene anayikidwa ndi mafumu a Yuda kuti azifukiza lubani ku malo opembedzera mafano a ku mizinda ya ku Yuda ndi kumalo ozungulira Yerusalemu, amene ankafukiza lubani kwa Baala, dzuwa, mwezi, nyenyezi ndi zinthu zonse zamlengalenga. Anachotsa fano la Asera mʼNyumba ya Yehova napita nalo kunja kwa Yerusalemu, ku Chigwa cha Kidroni, nalitentha kumeneko. Anapera fanolo ndi kukataya phulusa lake pa manda a anthu wamba. Iye anagwetsanso tinyumba ta ochita zachiwerewere, timene tinali mʼNyumba ya Yehova, kumene akazi ankalukirako mikanjo yovala popembedza Asera.
Yosiya anabweretsanso ansembe onse kuchokera mʼmizinda ya Yuda, nawononga malo opembedzera mafano, kuyambira ku Geba mpaka ku Beeriseba, kumene ansembe ankafukizako lubani. Anagwetsa nyumba za milungu zimene zinali pa chipata cha Yoswa, bwanamkubwa wa mzindawo, kumanzere kwa chipata cha mzinda. Ngakhale kuti ansembe a ku malo opembedzera mafanowo sanawalole kuti atumikire pa guwa lansembe la Yehova mu Yerusalemu, koma ankadya buledi wopanda yisiti pamodzi ndi ansembe anzawo.
Mfumu Yosiya anawononganso Tofeti, amene anali ku Chigwa cha Hinomu, kuti wina aliyense asagwiritse ntchito malowo popereka mwana wake wamwamuna kapena wamkazi pa moto kwa Moleki. Anachotsa pa chipata cholowera ku Nyumba ya Yehova akavalo amene mafumu a Yuda anawapereka ngati nsembe kwa dzuwa. Akavalo anali pafupi ndi bwalo la chipinda cha mkulu wina wotchedwa Natani-Meleki. Ndipo Yosiya anatentha magaleta opembedzera dzuwa.
Anagwetsa maguwa amene mafumu a Yuda anawamanga pa denga pafupi ndi chipinda chapamwamba cha Ahazi, ndiponso maguwa amene Manase anamanga mʼmabwalo awiri a Nyumba ya Yehova. Yosiya anawachotsa kumeneko nawaphwanya ndi kutaya zidutswa zake mʼChigwa cha Kidroni. Mfumuyo inawononga malo opembedzera mafano amene ali kummawa kwa Yerusalemu cha kumpoto kwa Phiri la Chiwonongeko. Maguwawa Solomoni mfumu ya Israeli inamangira Asitoreti, fano lalikazi lonyansa la Asidoni, Kemosi, fano lonyansa la Amowabu, ndi Moleki, fano lonyansa la anthu a ku Amoni. Yosiya anaphwanya miyala ya chipembedzo ndiponso anadula mitengo ya fano la Asera ndipo anakwirira malowo ndi mafupa a anthu.
Ngakhalenso guwa lansembe la ku Beteli, malo opembedzera mafano amene anapanga Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli, Yosiya anawononga guwalo ndi malo opembedzera mafanowo. Iye anatentha malo opembedzera mafanowo ndi kuwapera ndipo anatenthanso fano la Asera. Kenaka Yosiya anayangʼanayangʼana ndipo ataona manda amene anali pomwepo, mʼmbali mwa phiri, analamula kuti afukule mandawo ndi kutulutsa mafupa kuti awatenthe paguwapo kuti alidetse, potsatira mawu a Yehova amene munthu wa Mulungu analoseratu za zimenezi.
Mfumu inafunsa kuti, “Kodi chizindikiro cha manda chimene ndikuwaonawo ndi chayani?”
Anthu a mu mzindamo anayankha kuti, “Ndi chizindikiro cha manda a munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda amene ananeneratu zimene inu mwalichita guwa lansembe la Beteli.”
Mfumuyo inati, “Alekeni manda amenewo, munthu asachotse mafupa ake.” Choncho anawasiya mafupa akewo pamodzi ndi mafupa a mneneri wa ku Samariya uja.
Monga momwe Yosiya anachitira ku Beteli, anachotsa ndi kuwononga nyumba za milungu zonse ndi malo opembedzera mafano amene mafumu anamanga mʼmizinda ya ku Samariya omwe anakwiyitsa Yehova. Yosiya anapha ansembe onse amene ankatumikira ku malo opembedzera mafano, anawaphera pa maguwa awo ndi kutentha mafupa awo. Kenaka iye anapita ku Yerusalemu.
Mfumu inalamula anthu onse kuti, “Chitani Chikondwerero cha Paska kulemekeza Yehova Mulungu wanu, motsatira zomwe zalembedwa mʼBuku la Chipangano.” Paska yotere inali isanachitikepo kuyambira nthawi ya oweruza amene anatsogolera Israeli, kapenanso nthawi yonse ya mafumu a Yuda sipanachitikenso Paska ngati imeneyo. Koma mʼchaka cha 18 cha Mfumu Yosiya, Paska imeneyi anachitira Yehova mu Yerusalemu.
Kuwonjezera apa, Yosiya anachotsa anthu a mawula, woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, milungu ya mʼnyumba, mafano ndiponso zinthu zonse zonyansa zopezeka mu Yuda ndi Yerusalemu. Iye anachita izi pokwaniritsa lamulo lolembedwa mʼbuku limene Hilikiya analipeza mʼNyumba ya Yehova. Yosiyayo asanalowe ufumu, ngakhale atamwalira, panalibenso mfumu ina yofanana naye imene inatembenukira kwa Yehova monga anachitira, ndi mtima wake wonse, ndi moyo wake wonse, ndi mphamvu zake zonse, motsatira Malamulo onse a Mose.
Komabe Yehova sanachotse mkwiyo wake woopsa, umene anali nawo pa Yuda chifukwa cha zonse zimene anachita Manase poputa mkwiyo wa Mulungu. Choncho Yehova anati, “Ndidzawachotsanso anthu a ku Yuda pamaso panga monga ndinachotsera anthu a ku Israeli ndipo ndidzawukana mzinda wa Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha, pamodzi ndi Nyumba ino imene ndinati, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo.’ ”
Ntchito zina za Yosiya ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda?
Yosiya akanali mfumu, Farao wotchedwa Neko, mfumu ya Igupto, anapita ku Mtsinje wa Yufurate kukathandiza mfumu ya ku Asiriya. Mfumu Yosiya anapita kukachita naye nkhondo, koma Neko anakumana naye ndi kumupha ku Megido. Atumiki a Yosiyayo ananyamula mtembo wake mu galeta kuchokera ku Megido mpaka ku Yerusalemu ndipo anamuyika mʼmanda akeake. Ndipo anthu a mʼdzikomo anatenga Yehowahazi mwana wa Yosiya namudzoza, ndipo iye analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.
Yehowahazi Mfumu ya Yuda
Yehowahazi anakhala mfumu ali ndi 23 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Hamutali, mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake. Farao Neko anamuyika mʼndende ku Ribula mʼdziko la Hamati kuti asalamulirenso mu Yerusalemu. Farao analamula Yuda kuti azikhoma msonkho wa siliva wolemera makilogalamu 3,400, ndiponso golide wolemera makilogalamu 34. Farao Neko anayika Eliyakimu mwana wa Yosiya kuti akhale mfumu mʼmalo mwa abambo ake Yosiya, ndipo anasintha dzina lake kukhala Yehoyakimu. Koma iye anatenga Yehowahazi kupita naye ku Igupto ndipo anakafera kumeneko. Yehoyakimu anapereka kwa Farao Neko siliva ndi golide amene anamufuna uja. Koma kuti iye apereke zimenezi, amankhometsa msonkho mʼdziko mwakemo ndipo amalandira siliva ndi golide kuchokera kwa anthu a mʼdzikomo molingana ndi chuma cha munthu aliyense.
Yehoyakimu Mfumu ya Yuda
Yehoyakimu anali wa zaka 25 pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Zebuda, mwana wa Pedaya wa ku Ruma. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga momwe anachitira makolo ake.
Pa nthawi ya ulamuliro wa Yehoyakimu, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anadzathira nkhondo dzikolo ndipo Yehoyakimu anakhala pansi pa ulamuliro wake zaka zitatu. Koma kenaka anasintha maganizo ake nawukira Nebukadinezara. Yehova anatumiza magulu a Ababuloni, Aaramu, Amowabu ndi Aamoni, kudzathira nkhondo Yuda. Iye anawatumiza kudzawononga Yuda molingana ndi mawu amene Yehova ananeneratu kudzera mwa aneneri ake. Ndithu, izi zinachitikira Yuda monga momwe Yehova analamulira nʼcholinga choti awachotse pamaso pake chifukwa cha machimo a Manase ndi zonse zimene anachita, kuphatikizapo kukhetsa magazi a anthu osalakwa. Chifukwa iye anadzaza Yerusalemu ndi magazi a anthu osalakwa ndipo Yehova sanafune kumukhululukira.
Ntchito zina za Yehoyakimu ndi zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Yehoyakimu anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Yehoyakini mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Mfumu ya Igupto sinatulukenso mʼdziko lake chifukwa mfumu ya Babuloni inalanda mayiko onse kuchokera ku Mtsinje wa ku Igupto mpaka ku Mtsinje wa Yufurate.
Yoyakini Mfumu ya Yuda
Yehoyakini anakhala mfumu ali ndi zaka 18 ndipo analamulira mu Yerusalemu miyezi itatu. Amayi ake anali Nehusita mwana wa Elinatani wa ku Yerusalemu. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira abambo ake.
Nthawi imeneyo ankhondo a Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ku Yerusalemu nazinga mzindawo ndi misasa ya nkhondo ndipo Nebukadinezara anafika ku mzindawo pamene ankhondo ake anawuzinga. Yehoyakini mfumu ya Yuda pamodzi ndi amayi ake, atumiki ake, anthu ake olemekezeka ndiponso akuluakulu onse anadzipereka kwa mfumu ya ku Babuloni.
Mfumu ya Babuloni inagwira Yoyakini ukapolo mʼchaka chachisanu ndi chitatu cha ufumu wake. Monga ananenera Yehova, Nebukadinezara anachotsa chuma chonse cha mʼNyumba ya Yehova ndiponso cha mʼnyumba ya mfumu ndipo anatenga ziwiya zonse zagolide za ku Nyumba ya Yehova zimene Solomoni mfumu ya Israeli anapanga. Anatenga anthu onse a mu Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo. Akuluakulu onse pamodzi ndi anthu ankhondo, anthu onse aluso ndi amisiri osula onse pamodzi analipo 10,000. Osauka okha ndiye anatsala mʼdzikomo.
Nebukadinezara anatenga Yehoyakini ngati kapolo kupita naye ku Babuloni. Mu Yerusalemu anatenganso amayi a mfumu, akazi ake, akuluakulu ake ndiponso anthu olemekezeka mʼdzikomo. Mfumu ya Babuloni inatumizanso ku Babuloni anthu ankhondo 70,000, anthu amphamvu ndi okonzeka kupita ku nkhondo, anthu aluso ndi amisiri osula 1,000. Iye analonga ufumu Mataniya, malume wa Yoyakini mʼmalo mwake ndipo anasintha dzina lake kuti akhale Zedekiya.
Zedekiya Mfumu ya Yuda
Zedekiya anakhala mfumu ali ndi zaka 21 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 11. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova monga anachitira Yehoyakimu. Zonsezi zinachitikira Yerusalemu ndi Yuda chifukwa cha mkwiyo wa Mulungu ndipo pa mapeto pake anawachotsa pamaso pake.
Kuwonongeka kwa Yerusalemu
Ndipo Zedekiya anawukira mfumu ya Babuloni.
Choncho mʼchaka chachisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anabwera ndi gulu lake lonse la ankhondo, nadzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Iye anamanga misasa kunja kwa mzindawo ndipo anamanga mitumbira ya nkhondo kuzungulira mzindawo. Mzindawo anawuzinga mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha Mfumu Zedekiya. Pa tsiku lachisanu ndi chinayi pa mwezi wachinayi, njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti anthu analibe chakudya. Pamenepo khoma la mzindawo linabowoledwa ndipo gulu lonse la ankhondo linathawa usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Iwo anathawira cha ku Araba, koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika. Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula, kumene anagamula mlandu wa Zedekiyayo. Iwo anapha ana a Zedekiya iyeyo akuona. Kenaka anakolowola maso a Zedekiya namumanga ndi unyolo wamkuwa ndi kupita naye ku Babuloni.
Mwezi wachisanu, pa tsiku lachisanu ndi chiwiri la mwezi, mʼchaka cha 19 cha Nebukadinezara, mfumu ya Babuloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, nduna ya mfumu ya Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. Iye anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu pamodzi ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse yofunika. Gulu lonse la ankhondo la ku Babuloni limene linali ndi mkulu wa asilikali oteteza mfumu ija, linagumula malinga ozungulira Yerusalemu. Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, ndi ena amene anathawira kwa mfumu ya Babuloni, pamodzi ndi ena onse kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. Koma mkulu wa asilikaliyo anasiya anthu ena osauka kwambiri mʼdzikomo kuti azisamalira minda ya mpesa ndi minda ina.
Ababuloni anaphwanya zipilala zamkuwa, maphaka ndiponso mbiya ya mkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova ndipo anatenga mkuwawo napita nawo ku Babuloni. Iwo anatenganso miphika, mafosholo, mbaniro za nyale, mbale ndi ziwiya zonse zamkuwa zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼNyumbayo. Mkulu wa asilikali uja anatenganso zofukizira lubani ndi mbale zowazira magazi. Zonsezi zinali zopangidwa ndi golide wabwino kwambiri kapena siliva.
Mkuwa wochokera ku zipilala ziwiri zija, mbiya ija ndi maphaka aja, zimene Solomoni anapanga mʼNyumba ya Yehova, kuchuluka kwake kunali kosawerengeka. Chipilala chilichonse chinali chotalika mamita asanu ndi atatu. Mutu wa mkuwa umene unali pamwamba pa chipilalacho unali mita imodzi ndi theka ndipo unakongoletsedwa ndi ukonde wa makangadza a mkuwa amene anazungulira mutuwo. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi chinacho, ndipo chinali ndi ukonde.
Mkulu wa asilikali uja anagwira ukapolo mkulu wa ansembe Seraya, Zefaniya wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apakhomo. Mwa anthu amene anali mu mzindamo, anatenga mkulu amene ankalamulira ankhondo ndiponso alangizi asanu a mfumu. Anatenganso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo amene ankalemba anthu ntchito ya usilikali mʼdzikomo pamodzi ndi anthu ake 60 amene anali mu mzindamo. Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja anawatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya Babuloni ku Ribula. Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloni inalamula kuti awakwapule ndi kuwapha.
Choncho Ayuda anatengedwa ukapolo kuwachotsa mʼdziko lawo.
Nebukadinezara mfumu ya Babuloni anasankha Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani, kukhala woyangʼanira anthu amene anatsala ku Yuda. Atsogoleri onse ankhondo ndi anthu awo atamva kuti mfumu ya Babuloni yasankha Gedaliya kukhala bwanamkubwa, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. Atsogoleriwo mayina awo anali awa: Ismaeli mwana wa Netaniya, Yohanani mwana wa Kareya, Seraya mwana wa Tanihumeti wa ku Netofa ndi Yaazaniya mwana wa Maakati, pamodzi ndi anthu awo. Gedaliya analumbira powatsimikizira iwo ndi anthu awo. Iye anati, “Musachite mantha ndi atsogoleri Ababuloniwa. Khalani mʼdziko muno ndipo tumikirani mfumu ya Babuloni. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino.”
Koma pa mwezi wachisanu ndi chiwiri, Ismaeli mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, wa banja laufumu, anabwera ndi anthu khumi ndipo anapha Gedaliya pamodzi ndi Ayuda ndi anthu a ku Babuloni amene anali naye limodzi ku Mizipa. Chifukwa cha zimenezi, anthu onse kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo anathawira ku Igupto chifukwa choopa Ababuloni.
Kumasulidwa kwa Yehoyakini
Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini mfumu ya Yuda, chaka chimene Evili-Merodaki anakhala mfumu ya Babuloni, anamasula Yehoyakini mʼndende pa mwezi wa 12 pa tsiku la 27. Anamukomera mtima namukweza kupambana mafumu ena onse amene anali naye ku Babuloni. Choncho Yoyakini anavula zovala zake za ku ndende, ndipo ankadya ndi mfumu masiku onse a moyo wake. Mfumu inkamupatsa Yehoyakini chakudya tsiku lililonse pa moyo wake wonse.