- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
2 AKORINTO
Kalata Yachiwiri ya Paulo Yolembera Akorinto
2 Akorinto
2 Ako
KALATA YACHIWIRI YA PAULO YOLEMBERA
AKORINTO
Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, pamodzi ndi mʼbale wathu Timoteyo,
Kulembera mpingo wa Mulungu mu Korinto, pamodzi ndi oyera mtima onse mu Akaya monse.
Mukhale ndi chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.
Mulungu Mwini Chitonthozo
Alemekezeke Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu, Atate achifundo chonse, Mulungu wachitonthozo chonse. Iye amatitonthoza ife mʼmavuto athu onse, kuti ifenso tithe kutonthoza amene ali pavuto lililonse ndi chitonthozo chimene ife tilandira kwa Mulungu. Pakuti monga momwe tili mʼmasautso pamodzi ndi Khristu, momwemonso Khristu amatitonthoza kwambiri. Ngati ife tikusautsidwa, nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe ndi kupulumutsidwa. Ngati ife tikutonthozedwa nʼchifukwa choti inu mutonthozedwe, ndi chitonthozo chimene chimabweretsa mwa inu kupirira kosawiringula pa zosautsa zomwe timasauka nazo ife. Ndipo chiyembekezo chathu pa inu nʼcholimba chifukwa tikudziwa kuti monga momwe mumamva zowawa pamodzi nafe, momwemonso mumatonthozedwa nafe pamodzi.
Abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa za masautso amene tinakumana nawo mʼchigawo cha Asiya. Tinapanikizidwa koopsa kuposa muyeso woti nʼkutha kupirira, mwakuti sitinkadziwa kuti nʼkukhalabe ndi moyo. Zoonadi, tinamva mʼmitima mwathu chilango cha imfa. Koma izi zimachitika kuti tisangodzidalira mwa ife tokha koma Mulungu yemwe amaukitsa akufa. Mulungu watilanditsa ku zoopsa zotere za imfa, ndipo adzatilanditsanso. Ife tayika chiyembekezo chathu pa Iyeyo kuti adzapitiriza kutilanditsabe. Mutithandize potipempherera. Pamenepo ambiri adzathokoza mʼmalo mwathu, chifukwa cha chisomo chake poyankha mapemphero a anthu ambiri.
Paulo Afotokoza za Kusintha kwa Ulendo Wake
Tsono chonyadira chathu nʼchakuti, chikumbumtima chathu chimatitsimikizira kuti timakhala bwino mʼdziko lapansi, makamaka pa ubale wathu ndi inu. Takhala moona mtima ndi oyera mtima. Sitinachite chomwechi mwa nzeru ya dziko lapansi koma monga mwa chisomo cha Mulungu. Pakuti sitikukulemberani zoti simungawerenge kapena kumvetsetsa. Monga mwamva pangʼono chabe, ndikuyembekeza kuti mudzamvetsa kwenikweni, kuti mutha kutinyadira monga ife tidzakunyadirani, pa tsiku la Ambuye Yesu.
Popeza ndinatsimikiza mtima za ichi, nʼchifukwa chake ndinafuna kuti poyamba, ndidzakuchezereni kuti mupindule pawiri. Ndinafuna kuti ndidzakuchezereni pa ulendo wanga wopita ku Makedoniya ndi kudzakuonaninso pochokera ku Makedoniyako kuti inu mudzandithandize pa ulendo wanga wopita ku Yudeya. Kodi pamene ndinkakonzekera zimenezi, mukuganiza kuti ndinkachita mwachibwana? Kapena kuti ndinkaganiza ngati mwa dziko lapansi; kuti ndikhoza kumanena kuti, “Inde, Inde,” nthawi yomweyo nʼkumatinso “Ayi, Ayi?”
Koma zoona monga Mulungu ali wokhulupirika, uthenga wathu kwa inu siwakuti, “Inde” nʼkutinso “Ayi.” Pakuti Yesu Khristu mwana wa Mulungu amene ine, Silivano ndi Timoteyo tinamulalikira pakati panu sali “Inde” yemweyonso “Ayi.” Koma nthawi zonse mwa Iye muli “Inde.” Pakuti ngakhale malonjezo a Mulungu atachuluka chotani, onsewo ndi “Inde” mwa Khristu. Kotero kuti mwa Iye, ife timati “Ameni” kuchitira Mulungu ulemu. Tsono ndi Mulungu amene anachititsa kuti inu ndi ife tiyime molimba mwa Khristu. Anatidzoza ife, nayikanso Mzimu wake mʼmitima mwathu kutitsimikizira za mʼtsogolo.
Mulungu ndi mboni yanga kuti sindinabwererenso ku Korinto kuno kuti ndisakumvetseni chisoni. Sikuti ife tikufuna kukhala olamulira chikhulupiriro chanu, koma timagwira nanu ntchito pamodzi kuti mukhale achimwemwe, chifukwa ndinu okhazikika kwambiri mʼchikhulupiriro.
Kotero ndinatsimikiza maganizo anga kuti ndisachitenso ulendo wina owawa wobwera kwanuko. Pakuti ngati ndikumvetsani chisoni, kodi angandisangalatse ndani, kupatula inuyo amene ndakumvetsani chisoni? Nʼchifukwa chake ndinakulemberani monga ndinachitiramo kuti nditabwera kwanuko ndisadzamve chisoni ndi anthu oyenera kundisangalatsa. Ndinali ndi chikhulupiriro ndi inu nonse kuti inuyo mukakhala ndi chimwemwe poona kuti inenso ndili ndi chimwemwe. Pakuti ndinakulemberani kalata ija ndili wopsinjika ndi wowawidwa mtima kwambiri ndi kutuluka misozi yambiri, osati pofuna kukumvetsani chisoni koma kuti ndikudziwitseni kuti ndimakukondani kwambiri.
Za Kukhululukira Wolakwa
Koma ngati wina wamvetsa chisoni, sanamvetse chisoni ine ndekha, koma koposa mosawonjezera wakhumudwitsa nonsenu, kunenatu mosawonjezera. Chilango chimene ambiri a inu mwamupatsa munthu ameneyu nʼchokwanira. Mʼmalo mwake tsono, muyenera kumukhululukira ndi kumulimbikitsa mtima kuti asamve chisoni choposa muyeso, angataye mtima. Choncho ndikukupemphani kuti mutsimikizire chikondi chanu pa iye. Cholinga china chimene ndinakulemberani kalata ija chinali chofuna kukuonani ngati mudzandimvera pa zonse. Aliyense amene mumukhululukire, inenso ndimukhululukira. Ndipo ndikakhululukira, ngati pali kanthu koti ndikhululukire, ndiye kuti ndakhululuka chifukwa cha inu pamaso pa Khristu, kupewa kuti Satana angapezere mpata pa ife, pajatu timadziwa machenjerero ake.
Atumiki a Pangano Latsopano
Tsono nditafika ku Trowa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Khristu, nʼkupeza kuti Ambuye anditsekulira khomo, ndinasowa mtendere mu mtima mwanga, chifukwa sindinapezeko mʼbale wanga Tito. Choncho ndinatsanzikana ndi anthu kumeneko nʼkupita ku Makedoniya.
Koma tithokoze Mulungu amene amatitsogolera nthawi zonse monga ogwidwa ku nkhondo a Khristu pa chipambano chake. Tsono amatigwiritsa ntchito yofalitsa ponseponse nzeru zodziwira Khristu ngati fungo labwino. Pakuti kwa Mulungu ndife fungo labwino la Khristu pakati pa iwo amene akupulumutsidwa ndi amene akuwonongeka. Kwa amene akuwonongeka ndife fungo la imfa, limawapha. Ndipo kwa amene akupulumuka ndife fungo lamoyo, limawapatsa moyo. Ndani angayithe ntchito yotereyi? Kusiyana ndi ena ambiri, ife sitilalikira Mawu a Mulungu kuti tipeza phindu. Mʼmalo mwake, ife mwa Khristu timayankhula pamaso pa Mulungu moona mtima, monga anthu otumidwa ndi Mulungu.
Akhristu ndi Kalata Yochokera kwa Khristu
Kodi tayambanso kudzichitira umboni tokha? Kapena kodi ifenso tikufuna makalata otivomereza kwa inu, kapena ochokera kwa inu monga anthu ena? Inu ndinu kalata yathu, yolembedwa pa mitima yathu, yodziwika ndi yowerengedwa ndi aliyense. Inu mukuonetsa kuti ndinu kalata yochokera kwa Khristu, zotsatira za utumiki wathu, osati yolembedwa ndi inki koma ndi Mzimu wa Mulungu wamoyo, osati pa miyala yosemedwa koma mʼmitima ya anthu.
Kulimba mtima kumeneku tili nako pamaso pa Mulungu kudzera mwa Khristu. Sikuti mwa ife muli kanthu kotiganizitsa kuti tingathe kugwira ntchitoyi patokha, koma kulimba mtima kwathu kumachokera kwa Mulungu. Iye watipatsa kulimba mtima kuti tikhale atumiki a pangano latsopano, osati malamulo olembedwa koma a Mzimu; pakuti malamulo olembedwa amapha koma Mzimu amapereka moyo.
Ulemerero wa Pangano Latsopano
Koma ngati utumiki umene unabweretsa imfa uja, wolembedwa ndi malemba pa mwalawu, unabwera ndi ulemerero mwakuti Aisraeli sanathe kuyangʼanitsitsa nkhope ya Mose chifukwa cha ulemerero wa pa nkhopeyo, ngakhale kuti unali kunka nuzilala, kodi nanga utumiki wa Mzimu sudzaposa apa? Ngati utumiki umene umatsutsa anthu unali ndi ulemerero, nanga koposa kotani ulemerero wa utumiki wobweretsa chilungamo! Pakuti zimene zinali ndi ulemerero, tsopano zilibenso ulemerero pofananitsa ndi ulemerero wopambanawo. Ndipo ngati zosakhalitsa zinabwera ndi ulemerero, koposa kotani ulemerero wamuyayawo!
Choncho, popeza tili ndi chiyembekezo chotere, ndife olimba mtima kwambiri. Ife sitili ngati Mose amene amaphimba nkhope yake kuopa kuti Aisraeli angaone kuti kunyezimira kwa nkhope yake kumazilala. Koma nzeru zawo zinawumitsidwa, pakuti mpaka lero chophimbira chomwecho chikanalipo pamene akuwerenga Chipangano Chakale. Sichinachotsedwebe, chifukwa chimachotsedwa ngati munthuyo ali mwa Khristu yekha. Ngakhale lero lomwe lino akuwerenga mabuku a Mose pali chophimbabe mitima yawo. Koma pamene aliyense atembenukira kwa Ambuye, “chophimbacho chimachotsedwa.” Tsono Ambuye ndi Mzimu, ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye, pali ufulu. Ife tonse, amene ndi nkhope zosaphimba timaonetsera ulemerero wa Ambuye, tikusinthika kufanana ndi ulemerero wake, umene ukunka nuchulukirachulukira, wochokera kwa Ambuye, amene ndi Mzimu.
Chuma Chosungidwa Mʼmbiya Zadothi
Choncho popeza mwachifundo cha Mulungu tili ndi utumiki uwu, sititaya mtima. Koma ife takaniratu njira zonse zachinsinsi ndi zochititsa manyazi. Sitichita kanthu mwachinyengo kapena mopotoza Mawu a Mulungu. Mʼmalo mwake, timayankhula choonadi poyera pamaso pa Mulungu, kufuna kuti aliyense ativomereze mu mtima mwake. Koma ngakhale uthenga wathu wabwino utakhala wophimbika, ndi wophimbika kwa okhawo amene akutayika. Mulungu wa dziko lapansi anachititsa khungu anthu osakhulupirira, kuti asathe kuona kuwala kwa Uthenga Wabwino umene umaonetsa ulemerero wa Khristu, amene ndi chifaniziro cha Mulungu. Choncho sitilalikira za ife eni, koma Yesu Khristu monga Ambuye, ife ndife atumiki anu chifukwa cha Yesu. Pakuti Mulungu amene anati, “Kuwala kuwunike kuchokera mu mdima,” Iyeyo ndiye anawunikira mʼmitima mwathu kutipatsa kuwala kuti tidziwe ulemerero wa Mulungu umene ukuoneka pa nkhope ya Yesu Khristu.
Koma tili ndi chuma ichi mʼmbiya zadothi, kusonyeza kuti mphamvu yoposayi, imachokera kwa Mulungu osati kwa ife. Tapanikizika kwambiri mbali zonse koma osaphwanyika; tathedwa nzeru koma osataya mtima; tazunzidwa, koma osasiyidwa; takanthidwa, koma osawonongeka. Nthawi zonse tikuyenda nayo imfa ya Yesu mʼthupi mwathu, kuti moyo wake Yesu uwonekenso mʼthupi mwathu. Pakuti nthawi zonse, ngakhale tili ndi moyo, tikuperekedwa ku imfa chifukwa cha Yesu, kuti moyo wake wa Yesu uwonekenso mʼmatupi mwathu amene amafa. Choncho imfa ikugwira ntchito mwa ife, koma moyo ukugwira ntchito mwa inu.
Kwalembedwa kuti, “Ndinakhulupirira; nʼchifukwa chake ndinayankhula.” Popeza ife tili ndi mtima womwewo wokhulupirira, ifenso timakhulupirira ndi kuyankhula, chifukwa timadziwa kuti amene anaukitsa Ambuye Yesu kwa akufa adzatiukitsanso ife pamodzi ndi Yesu, natipereka ife ndi inu pamaso pake. Zonsezi nʼkuti inu mupindule, kuti chisomochi chifikire anthu ochuluka kwambiri, amenenso adzathokoza mochuluka kwambiri ndi kupereka ulemerero kwa Mulungu.
Nʼchifukwa chake ife sititaya mtima. Ngakhale thupi lathu likunka lifowokerafowokera, koma mʼkatimu tikulimbikitsidwa mwatsopano tsiku ndi tsiku. Pakuti masautso athu ndi opepuka ndi a kanthawi, koma akutitengera ulemerero wamuyaya umene ndi wopambana kwambiri. Motero sitiyangʼana zinthu zimene ndi zooneka ndi maso, koma zinthu zimene ndi zosaoneka. Pakuti zimene zimaoneka ndi zosakhalitsa, koma zimene sizioneka ndi zamuyaya.
Matupi Atsopano
Popeza tikudziwa kuti ngati msasa wa dziko lapansi umene tikukhalamo uwonongeka, tili ndi nyumba yochokera kwa Mulungu, nyumba yamuyaya yakumwamba, osati yomangidwa ndi manja a anthu. Pakali pano tibuwula, ndi kulakalaka kuvala nyumba yathu ya kumwambayo, chifukwa tikavala, sitidzapezekanso amaliseche. Pamene tili mu msasa uno, timalemedwa ndipo timabuwula, chifukwa sitifuna kukhala amaliseche koma ovala nyumba yathu ya kumwamba, kuti chimene chili chakufa chimezedwe ndi moyo. Tsono ndi Mulungu amene anatikonzeratu ife kuti tilandire zimenezi. Iye anatipatsa Mzimu ngati chikole, kutsimikizira zimene zikubwera.
Nʼchifukwa chake nthawi zonse timalimba mtima, ndipo timadziwa kuti pamene tikukhala mʼthupi, ndiye kuti tili kutali ndi Ambuye. Ife timakhala mwachikhulupiriro, osati mwa zooneka ndi maso. Inde, ife tikulimba mtima, ndipo tikanakonda kulekana nalo thupi lathu ndi kukhala ndi Ambuye. Choncho timayesetsa kukondweretsa Ambuye, ngakhale tikhale mʼthupi, kapena tichokemo. Pakuti tonsefe tiyenera kukaonekera pa mpando woweruza wa Khristu, kuti aliyense wa ife akalandire zomuyenera molingana ndi zimene anachita ali mʼthupi; zabwino kapena zoyipa.
Ntchito Yoyanjanitsa
Tsono popeza tikudziwa tanthauzo la kuopa Ambuye, ife timayesetsa kukopa anthu. Mulungu amatidziwa bwino lomwe, ndipo tikukhulupirira kuti inunso mumatidziwa bwino mʼmitima mwanu. Sitikudzichitiranso tokha umboni kwa inu, koma tikukupatsani mwayi oti muzitinyadira. Tikufuna kuti muwayankhe amene amanyadira zinthu zooneka ndi maso osati zimene zili mu mtima. Ngati ndife amisala, monga amanenera ena, nʼchifukwa chofuna kuti Mulungu alemekezedwe. Ngati si ife amisala, nʼkuti inu muthandizike. Pakuti chikondi cha Khristu ndicho chimatikakamiza, chifukwa tikutsimikiza kuti mmodzi anafera anthu onse, kotero kuti anthu onse anafanso. Ndipo Iye anafera anthu onse kuti amene ali ndi moyo, asakhale ndi moyo wofuna kudzikondweretsa okha, koma azikondweretsa amene anawafera naukitsidwa chifukwa cha iwowo.
Choncho, kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo ife sitiganizirapo za munthu aliyense monga mwanzeru za umunthu, ngakhale kuti poyamba tinkaganiza za Khristu mʼnjira imeneyi, koma tsopano sititeronso. Nʼchifukwa chake, ngati munthu aliyense ali mwa Khristu, ndi wolengedwa kwatsopano; zinthu zakale zapita taonani, zakhala zatsopano. Zonsezi zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa ndi Iye mwini kudzera mwa Khristu ndipo anatipatsa ife utumiki wa chiyanjanitso. Mulungu ankayanjanitsa dziko lapansi kwa Iye mwini kudzera mwa Khristu, osawerengera anthu monga mwa zochimwa zawo. Ndipo watisungitsa ife uthenga uwu wa chiyanjanitso. Choncho ife ndi akazembe a Khristu, monga ngati Mulungu akudandaulira anthu kudzera mwa ife. Ife tikukupemphani inu mʼmalo mwa Khristu kuti, yanjanitsidwani ndi Mulungu. Chifukwa cha ife, Mulungu anasandutsa wopanda tchimoyo kukhala tchimo, kuti mwa Iye ife tikakhale chilungamo cha Mulungu.
Pogwira naye ntchito pamodzi, tikukudandaulirani kuti musangolandira chisomo cha Mulungu pachabe. Pakuti akunena kuti,
“Pa nthawi yanga yabwino yokomera anthu mtima ndinakumvera,
ndipo pa nthawi yopulumutsa ndinakuthandiza.
Taonani, ndikukuwuzani kuti, ino ndiyo nthawi yabwino ya Ambuye, lero ndiye tsiku la chipulumutso.”
Masautso a Paulo
Ife sitikuyika chokhumudwitsa pa njira ya wina aliyense, kuti utumiki wathu usanyozeke. Mʼmalo mwake, mwanjira iliyonse timasonyeza kuti ndife atumiki a Mulungu popirira kwambiri mʼmasautso, mʼzowawa ndi mʼzodetsa nkhawa. Pomenyedwa, kuponyedwa mʼndende ndi mʼzipolowe. Pogwira ntchito mwamphamvu, posagona usiku onse, posowa chakudya; pokhala moyo woyera mtima, pomvetsa zinthu, wokoma mtima ndi wachifundo mwa Mzimu Woyera ndi mwachikondi choonadi ndi poyankhula choonadi mwamphamvu ya Mulungu. Zida zimene zili mʼdzanja lamanja ndi lamanzere ndizo chilungamo. Timatumikira Mulungu ngakhale ena amatinyoza ndi ena amatilemekeza, ena amatinenera chipongwe, enanso amatiyamikira. Ena amatitenga kukhala ngati onena zoona, ndipo enanso amatitenga kukhala ngati onena zabodza. Amatiyesa osadziwika komatu ndife odziwika kwambiri. Amatiyesa wooneka ngati tikufa, koma tikupitirirabe ndi moyo, okanthidwa, koma osaphedwa. Amatiyesa achisoni, koma ndife achimwemwe nthawi zonse, aumphawi, koma olemeretsa ambiri; wopanda kanthu, koma tili ndi zonse.
Tayankhula momasuka kwa inu, Akorinto, ndipo tanena zonse za kumtima kwathu. Ife sitikukubisirani chikondi chathu pa inu, koma inu mukubisa chikondi chanu pa ife. Pofuna kufanana zochita ndi kuyankhula monga kwa ana anga, nanunso muzinena za kukhosi kwanu.
Kukhala Pamodzi ndi Osakhulupirira
Musamasenze goli pamodzi ndi osakhulupirira. Kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kulungama ndi kusalungama? Kapena kodi pali mgwirizano wanji pakati pa kuwala ndi mdima? Pali mgwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali? Kapena munthu wokhulupirira angayanjane bwanji ndi munthu wosakhulupirira? Pali mgwirizano wanji pakati pa Nyumba ya Mulungu ndi nyumba ya mafano? Popezatu ndife Nyumba ya Mulungu wamoyo. Monga Mulungu wanena kuti,
“Ndidzakhala mwa iwo
ndipo ndidzayendayenda pakati pawo,
ndipo ndidzakhala Mulungu wawo,
ndipo adzakhala anthu anga.”
Nʼchifukwa chake
“Tulukani pakati pawo
ndi kudzipatula,
akutero Ambuye.
Musakhudze chodetsedwa chilichonse,
ndipo ndidzakulandirani.”
Ndipo
“Ndidzakhala Atate anu,
ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi aakazi,
akutero Ambuye, Wamphamvuzonse.”
Abwenzi okondedwa, popeza tili ndi malonjezo amenewa, tiyeni tidziyeretse, kusiyana nazo zilizonse zimene zikhoza kudetsa thupi ndi mzimu, ndipo tiyesetse kukhala oyera mtima poopa Mulungu.
Chimwemwe cha Paulo
Mutipatse malo mʼmitima mwanu. Ife sitinalakwire munthu aliyense, kapena kuyipitsa munthu aliyense, kapena kumuchenjerera munthu aliyense. Sindikunena izi kuti mupezeke olakwa. Ndinanena kale kuti ife timakuganizirani kwambiri kotero kuti tili pamodzi, ngakhale tikhale moyo kapena timwalire. Ndimakukhulupirirani kwambiri ndipo ndimakunyadirani kwambiri. Ndikulimbikitsidwa kwambiri; mʼmasautso athu onse, chimwemwe changa chilibe malire.
Pakuti titafika ku Makedoniya, sitinapume nʼkomwe, koma tinavutitsidwa mbali zonse. Kunja kunali mikangano, ndipo mʼmitima mwathu munali mantha. Koma Mulungu, amene amatonthoza mtima wopsinjika, anatitonthoza mtima ndi kufika kwa Tito, sikubwera kwake kokhako, komanso mawu achilimbikitso amene analandira kuchokera kwa inu. Iye anatiwuza kuti mukufuna kundiona, zachisoni chanu chachikulu, ndi kudzipereka kwanu kwa ine, motero chimwemwe changa chinachuluka kuposa kale.
Ngakhale kalata yanga ija inakupwetekani mtima, sindikudandaula kuti ndinalemberanji. Ngakhale zinandikhudza, ndikudziwa kuti kalata yanga inakupwetekani, koma kwa kanthawi kochepa. Koma tsopano ndine wokondwa, osati chifukwa chakuti kalatayo inakupwetekani, koma chifukwa chakuti chisoni chanu chinakuthandizani kutembenuka mtima. Pakuti munamva chisoni monga mmene Mulungu amafunira, choncho simunapwetekedwe mwanjira iliyonse. Chisoni chimene Mulungu amafuna chimabweretsa kutembenuka mtima komwe kumabweretsa chipulumutso, ndipo sichikhumudwitsa. Koma chisoni cha dziko lapansi chimabweretsa imfa. Taonani zimene chisoni chimene Mulungu amafuna chatulutsa mwa inu. Chatulutsa khama lalikulu, chakuthandizani kuti mudzikonze nokha, chakukwiyitsani kwambiri, komanso chakupatsani mantha aakulu. Chakuchititsani kuti mufune kundiona ine, mwakhudzidwa kwambiri ndipo mukufuna kuonetsetsa kuti chilungamo chachitikadi. Pa nkhani yonseyi, mwaonetsadi kuti ndinu osalakwa. Choncho ngakhale ndinakulemberani kalata ija, sindinayilembe ndi chifukwa cha amene analakwayo kapena wolakwiridwa, koma ndinayilemba kuti inuyo muone kudzipereka kwanu kwa ife pamaso a Mulungu. Zimenezi zatilimbikitsa kwambiri.
Kuwonjezera pa zotilimbikitsazo, tinakondwa kwambiri poona chisangalalo cha Tito, chifukwa nonsenu munamuthandiza kukhazikitsa mtima wake pansi. Ndinamuwuza kuti ndimakunyadirani, ndipo simunandichititse manyazi. Koma monga zonse zimene tinakuwuzani zinali zoona, tsono zomwe ndinawuza Tito zokunyadirani zinali zoona. Ndipo chikondi chake pa inu nʼchachikulu kwambiri akakumbukira kuti nonse munali omvera, munamulandira ndi mantha ndi kunjenjemera. Ndine wokondwa kuti ndingathe kukukhulupirirani pa zonse.
Kulimbikitsa Zopereka
Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu. Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.
Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.
Ndipo nawa malangizo anga pa zoyenera inu kuchita pa nkhaniyi. Chaka chatha munali oyamba, osati ongofuna kupereka kokha komanso okhala ndi mtima ofuna kupereka. Tsopano tsirizani ntchitoyi, ndipo changu chanu chofunitsitsa kugwira ntchitoyi ndi kuyitsiriza chichitike molingana ndi zimene muli nazo. Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.
Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.”
Tito Atumidwa ku Korinto
Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu. Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.
Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu. Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.
Nʼkosafunika kuti ndikulembereni za utumiki othandiza anthu a Mulungu. Popeza ndikudziwa mtima wanu wofuna kuthandiza, ndipo ndakhala ndikuwawuza monyadira a ku Makedoniya za chimenechi. Ndimawawuza kuti inu a ku Akaya munakonzeka kale chaka chatha kuti mupereke. Ndipo changu chanu chapatsa chidwi ambiri mwa iwo kuti nawonso achitepo kanthu. Koma ndikutumiza abalewo kuti kukunyadirani kwathu pa zimenezi kutsimikizike kuti si kwachabe ndi kuti mukhale okonzeka monga ndinanenera. Pakuti nditabwera kumeneko ndi abale ena a ku Makedoniya, ndikukupezani kuti simunakonzeke, tingadzachite manyazi chifukwa chokudalirani. Koma amene angadzachite manyazi kwambiri ndi inuyo. Choncho ndinaganiza kuti nʼkofunika kupempha abale kuti adzakuchezereni ineyo ndisanafike, ndikuti adzatsirize kukonzekera mphatso zomwe munalonjeza kupereka mowolowamanja. Motero mphatsoyo idzakhala yokonzeratu, ndipo idzakhala mphatso yoperekedwa mowolowamanja, osati mokakamizidwa.
Kupereka Mowolowamanja
Takumbukirani mawu awa: Amene adzala pangʼono, adzakololanso pangʼono, ndipo amene adzala zochuluka, adzakololanso zochuluka. Munthu aliyense apereke chimene watsimikiza mu mtima mwake kuti apereka, osati monyinyirika kapena mokakamizidwa, pakuti Mulungu amakonda wopereka mokondwera. Ndipo Mulungu akhoza kukudalitsani kwambiri, kuti inuyo nthawi zonse mukhale ndi zinthu zokukwanirani, ndiponso ndi zina zochuluka kuti muthandize pa ntchito zonse zabwino. Paja analemba kuti,
“Wopereka mphatso zake mowolowamanja kwa osauka,
chilungamo chake chimanka mpaka muyaya.”
Tsono Mulungu amene amapereka mbewu kwa wofesa, ndiponso chakudya kuti adye, adzaperekanso mbewu mʼnkhokwe zanu ndi kuzichulukitsa. Iye adzachulukitsanso zipatso za chilungamo chanu. Adzakulemeretsani pa zonse kuti mukhale owolowamanja pa nthawi zonse. Ndipo kuwolowamanja kwanu kudzera mwa ife, kudzakhala kuthokoza kwa Mulungu.
Ntchito imene mukugwirayi siyongothandiza kokha anthu a Mulungu kupeza zosowa, komanso ikuthandiza kuti anthu ambiri ayamike Mulungu. Chifukwa cha ntchito imene mwawatsimikizira nokha, anthu ena onse adzayamika Mulungu chifukwa cha kumvera kwanu kumene kumaonekera pamene mukuvomereza Uthenga Wabwino wa Khristu, ndiponso chifukwa chowagawira mowolowamanja iwowo pamodzi ndi wina aliyense. Ndipo iwowo adzakupemphererani mwachikondi chifukwa cha chisomo choposa chimene Ambuye wakupatsani. Tiyamike Mulungu chifukwa cha mphatso zake zosaneneka!
Paulo Ateteza Utumiki Wake
Mwa kufatsa ndi kuleza mtima kwa Khristu, ndikukupemphani, ine Paulo amene anthu ena amati ndimachita manyazi tikaonana maso ndi maso ndi inu, koma wosaopa pamene ndili kutali nanu! Ndikukupemphani kuti ndikadzafika kumeneko ndisadzachite kuyankhula mwamphamvu monga mmene ndimayembekezera kudzachita kwa anthu ena amene amaganiza kuti machitidwe athu ndi ofanana ndi anthu a dziko lapansi. Ngakhale ife timakhala mʼdziko lapansi, sitimenya nkhondo monga mmene dziko lapansi limachitira. Pakuti zida zathu zankhondo si zida za dziko lapansi. Koma ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu zotha kugwetsa malinga. Timagonjetsa maganizo onse onyenga ndiponso kudzikuza kulikonse kolimbana ndi anthu kuti asadziwe Mulungu. Ndipo timagonjetsa ganizo lililonse kuti limvere Khristu. Ndipo ife tidzakhala okonzeka kulanga aliyense wosamvera ngati inuyo mutakhala omvera kwenikweni.
Inu mukuweruza potengera zimene maso anu akuona. Ngati wina akutsimikiza kuti ndi wake wa Khristu, iye aganizenso kuti ifenso ndife a Khristu monga iye. Tsono ngakhale nditadzitama momasuka za ulamuliro umene Ambuye anatipatsa woti tikukuzeni osati kukuwonongani, ndithu sindidzachita manyazi. Ine sindikufuna kuoneka ngati ndikukuopsezani ndi makalata anga. Pakuti ena amati, “Makalata ake ndi awukali ndi amphamvu koma maonekedwe a thupi lake ndi wosagwira mtima ndipo mayankhulidwe ake ndi achabechabe.” Anthu oterewa ayenera kuzindikira kuti zomwe timalemba mʼmakalata tili kutali ndi zomwe tidzakhale tili komweko.
Sitikudziyika kapena kudzifananiza tokha ndi anthu ena amene amadziyenereza okha. Pamene akudzifanizira okha podziyerekeza ndi anzawo a mʼgulu lawo lomwe, ndi opanda nzeru. Komabe, ifeyo sitidzitama modutsa malire ake enieni, koma kudzitama kwathu kudzalekeza mʼmalire amene Mulungu anatiyikira, malire ake ndi mpaka kwa inu. Pakuti sitikudzitama modutsa malire ngati kuti sitinafike kwa inu, popeza tinali oyamba kufika kwa inu ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Choncho sitinyadiranso ntchito imene ena anayigwira. Chiyembekezo chathu nʼchakuti, pamene chikhulupiriro chanu chikukulirakulira, dera lathu la ntchito pakati panu lidzakulanso kwambiri, kuti tikalalikire Uthenga Wabwino mu zigawo zina kupitirira kwanuko. Pakuti sitikufuna kudzitama pa ntchito yogwira ena kale mʼdera la munthu wina. Koma, “Ngati munthu akufuna kunyadira, anyadire mwa Ambuye.” Pakuti munthu amene amavomerezedwa, si amene amadziyenereza yekha, koma munthu amene Ambuye amuyenereza.
Paulo ndi Atumwi Onyenga
Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani! Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro. Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu. Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta.
Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.” Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino. Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere? Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero. Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya. Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani!
Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira. Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu. Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo.
Paulo Anyadira Mazunzo Ake
Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono. Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi. Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi.
Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu. Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima?
Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga. Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire. Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.
Masomphenya a Paulo ndi Minga ya Mʼthupi Mwake
Ndiyenera kupitiriza kudzitamandira. Ngakhale palibe choti ndipindule, ndipitiriza kufotokoza za masomphenya ndi mavumbulutso ochokera kwa Ambuye. Ndikudziwa munthu mwa Khristu amene zaka khumi ndi zinayi zapitazo anatengedwa kupita kumwamba kwachitatu. Sindikudziwa ngati zinachitika ali mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. Ndipo ndikumudziwa munthu ameneyu. Sindikudziwa ngati zinachitika mʼthupi kapena ayi, zimenezo akudziwa ndi Mulungu. Munthuyu anatengedwa kupita ku paradizo. Ndipo anamva zinthu zosatheka kuneneka, zinthu zimene munthu saloledwa kunena. Ndidzatamanda za munthu ngati ameneyu, koma sindidzadzitamandira ine mwini kupatula za kufowoka kwanga. Ngakhale nditafuna kudzitamandira, sindingakhale chitsiru, chifukwa ndikunena zoona. Koma ndimapewa kuti pasapezeke munthu wondiganizira moposera chimene ndili chifukwa cha zimene ndimachita kapena kuyankhula, kapena chifukwa cha mavumbulutso aakulu kuposa awa. Choncho, kuti ndisadzitukumule, ndinayikidwa minga mʼthupi langa, wamthenga wa Satana, kuti adzindizunza. Katatu konse ndinapempha Ambuye kuti andichotsere. Koma anandiwuza kuti, “Chisomo changa ndi chokukwanira, pakuti mphamvu zanga zimaoneka kwathunthu mwa munthu wofowoka.” Choncho ndidzadzitamandira mokondwera chifukwa cha zofowoka zanga, kuti mʼkutero mphamvu ya Khristu ikhale pa ine. Tsono, chifukwa cha Khristu, ndimakondwera pamene ndili wofowoka, pamene akundinyoza, pamene ndikumva zowawa, ndi pamene akundizunza ndi kundisautsa. Pakuti pamene ndili wofowoka ndiye kuti ndili wamphamvu.
Paulo Akhudzidwa ndi Akorinto
Ndadzisandutsa wopusa, koma inu mwandichititsa zimenezi. Ndinu amene munayenera kundichitira umboni. Ngakhale kuti sindine kanthu, koma sindine wochepetsetsa kwa “atumwi apamwamba” aja. Ndinapirira pokuonetserani zizindikiro za mtumwi weniweni, pochita pakati panu zizindikiro, zodabwitsa ndi ntchito zamphamvu. Kodi inu munaoneka ochepa motani ku mipingo ina, kupatula kuti sindinali cholemetsa kwa inu? Mundikhululukire cholakwa chimenechi!
Ndakonzeka tsopano kudzakuyenderani kachitatu, ndipo sindidzakhala cholemetsa kwa inu chifukwa ndikungofuna inuyo osati zinthu zanu. Pakuti ana sasamalira makolo koma makolo ndiwo asamalira ana. Motero ndidzakondwera kukupatsani zanga zonse zimene ndili nazo ndi kudziperekanso ine mwini chifukwa cha inu. Kodi ine ndikamakukondani kwambiri chotere, inuyo mudzandikonda pangʼono? Ena mwa inu amavomereza kuti sindinali cholemetsa. Komabe ena amaganiza kuti ndine wochenjera, ndipo ndinakuchenjererani. Kodi ndinakudyerani masuku pamutu kudzera mwa wina aliyense amene ndinamutumiza kwa inu? Ndinamupempha Tito kuti abwere kwanuko ndipo ndinamutumiza pamodzi ndi mʼbale wathu. Kodi kapena Tito anakudyerani masuku pamutu? Kodi iye ndi ine sitinachite zinthu mofanana ndi Mzimu mmodzi yemweyo?
Kodi mukuyesa kuti nthawi yonseyi takhala tikudzitchinjiriza tokha? Takhala tikuyankhula pamaso pa Mulungu monga anthu amene ali mwa Khristu; ndipo abwenzi okondedwa, chilichonse chimene timachita ndi chofuna kukulimbikitsani. Pakuti ndikuona kuti pamene ndibwera sindidzakupezani monga mmene ndikufunira kuti muzikhalira, ndipo simungadzandione monga mmene mukufunira kundionera. Ndikuopa kuti pangadzakhale mkangano, nsanje, kupserana mitima, kugawikana, ugogodi, miseche, kudzitukumula ndi chisokonezo. Ndikuopa kuti pamene ndidzabwerenso, Mulungu adzandichepetsa pamaso panu, ndipo ndidzamva chisoni ndi ambiri amene anachimwa kale ndipo sanalape zonyansa, zachigololo ndi zilakolako zoyipa zimene anachita.
Mawu Otsiriza ndi Ochenjeza
Uwu ndi ulendo wachitatu ndikubwera kudzakuyenderani. “Nkhani itsimikizike ndi umboni wa anthu awiri kapena atatu.” Ndinakuchenjezani kale pamene ndinali nanu ulendo wachiwiri uja. Tsopano ndikubwereza ndisanafike. Ndikabweranso sindidzachitira chifundo amene anachimwa poyamba paja kapena wina aliyense amene anachimwa, popeza mufuna chitsimikizo chakuti Khristu akuyankhula kudzera mwa ine. Iye siwofowoka pofuna kuchita nanu koma ndi wamphamvu pakati panu. Pofuna kutsimikizira, anapachikidwa ali wofowoka koma ali ndi moyo mwamphamvu ya Mulungu. Chomwechonso, ife ndife ofowoka mwa Iye, koma tidzakhala ndi moyo pamodzi naye ndi mphamvu ya Mulungu, potumikira pakati panu.
Tadzisanthulani nokha kuti muone ngati muli mʼchikhulupiriro; dziyeseni nokha. Kodi simuzindikira kuti Khristu Yesu ali mwa inu, ngati si choncho mwalephera mayesowa? Ndipo ndikhulupirira kuti mudzazindikira kuti ife sitinalephere mayesowo. Tsopano tikupemphera kwa Mulungu kuti musadzachite kanthu kena kalikonse kolakwa. Osati chifukwa choti anthu aone kuti ife tapambana mayesowo koma kuti mudzachite zokhoza ngakhale anthu atamationa ngati olephera. Pakuti sitingachite chilichonse chotsutsana ndi choonadi, koma chokhacho chovomerezana ndi choonadi. Ife timasangalala kuti pamene tafowoka, inu muli amphamvu; ndipo pemphero lathu ndi lakuti mukhale angwiro. Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani.
Malonje Otsiriza
Potsiriza abale, ndikuti tsalani bwino. Yesetsani kukhala angwiro, mvetsetsani pempho langa, khalani a mtima umodzi, khalani mwamtendere. Ndipo Mulungu wachikondi ndi mtendere adzakhala nanu.
Lonjeranani ndi mpsopsono wachiyero. Anthu onse a Mulungu akupereka moni.
Chisomo cha Ambuye Yesu Khristu, ndi chikondi cha Mulungu, ndi chiyanjano cha Mzimu Woyera zikhale ndi inu nonse.