- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 1 TIMOTEYO Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Timoteyo 1 Timoteyo 1 Tim KALATA YOYAMBA YA PAULO YOLEMBERA TIMOTEYO Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa lamulo la Mulungu, Mpulumutsi wathu ndiponso Khristu Yesu chiyembekezo chathu. Kwa Timoteyo mwana wanga weniweni mʼchikhulupiriro. Chisomo, chifundo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu zikhale ndi iwe. Kutsutsa Aphunzitsi Onyenga Monga ndinakupempha pamene ndinkapita ku Makedoniya, khala ku Efeso komweko kuti uletse anthu ena kuphunzitsa ziphunzitso zonyenga, kapena kumangoyika mitima pa nthano zopeka ndi kufufuza za mayina a makolo awo. Zinthu zotere zimapititsa mʼtsogolo mikangano mʼmalo mwa ntchito ya Mulungu yomwe ndi ya chikhulupiriro. Cholinga cha lamuloli ndi chikondi, chomwe chimachokera mu mtima woyera, chikumbumtima chabwino ndi chikhulupiriro choona. Anthu ena anapatuka pa zimenezi ndipo anatsata nkhani zopanda tanthauzo. Iwo amafuna kukhala aphunzitsi amalamulo, koma sadziwa zimene akunena, kapena zimene akufuna kutsimikiza. Tikudziwa kuti Malamulo ndi abwino ngati munthu awagwiritsa ntchito bwino. Tikudziwanso kuti Malamulo sakhazikitsidwa chifukwa cha anthu olungama, koma ophwanya lamulo ndi owukira, osaopa Mulungu ndi ochimwa, wopanda chiyero ndi osapembedza; amene amapha abambo awo ndi amayi awo, kapena anthu ena. Malamulo amayikidwa chifukwa cha anthu achigololo ndi ochita zadama ndi amuna anzawo, anthu ogulitsa akapolo, abodza ndi olumbira zabodza, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona. Chiphunzitso chimene chimagwirizana ndi Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wodala, umene Iye mwini anandisungitsa. Chisomo cha Ambuye kwa Paulo Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene anandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Iye ananditenga kukhala wokhulupirira, nandipatsa ntchito mu utumiki wake. Ngakhale kuti kale ndinali wachipongwe, wozunza ndi wankhanza, anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita mwaumbuli ndi mopanda chikhulupiriro. Chisomo cha Ambuye athu chinatsanulidwa pa ine mochuluka, pamodzi ndi chikhulupiriro ndi chikondi zimene zili mwa Khristu Yesu. Mawu odalirika ndi woyenera kuwavomereza kwathunthu ndi awa: Yesu Khristu anabwera pa dziko lapansi kudzapulumutsa ochimwa, ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwitsitsa. Ndipo pa chifukwa chimenechi, Mulungu anandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwitsitsa, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse kuti ndikhale chitsanzo cha omwe angathe kumukhulupirira ndi kulandira moyo wosatha. Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Ameni. Ntchito ya Timoteyo Mwana wanga Timoteyo, ndikukupatsa langizo ili molingana ndi maulosi amene aneneri ananena za iwe. Pamene ukumbukira mawu amenewa udzatha kumenya bwino nkhondo utagwiritsitsa chikhulupiriro ndi chikumbumtima chabwino. Ena anazikana zimenezi motero chikhulupiriro chawo chinawonongeka. Ena mwa amenewa ndi Humenayo ndi Alekisandro, amene ndinawapereka kwa Satana kuti aphunzire kusachita chipongwe Mulungu. Malangizo Achipembedzo Tsono choyamba ndikukupemphani kuti mupempherere anthu onse. Mapemphero anu akhale opemba, opempha, opempherera ena ndi oyamika. Mupempherere mafumu ndi onse aulamuliro, kuti tikhale moyo wamtendere ndi bata, woopa Mulungu ndi oyera mtima. Izi ndi zabwino ndipo zimakondweretsa Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amafuna kuti anthu onse apulumutsidwe ndipo kuti adziwe choonadi. Pakuti pali Mulungu mmodzi yekha ndi Mʼkhalapakati mmodzi yekha pakati pa Mulungu ndi anthu, munthu uja Khristu Yesu. Iyeyu anadzipereka kukhala dipo lowombolera anthu onse. Umenewu ndi umboni umene waperekedwa mu nthawi yake yoyenera. Nʼchifukwa chake anandisankha kukhala mlaliki ndiponso mtumwi wophunzitsa anthu a mitundu ina mawu achikhulupiriro choona. Sindikunama ayi, ndikunena zoona. Choncho ndikufuna kuti paliponse popemphera, amuna azikweza manja awo kwa Mulungu mopanda mkwiyo kapena kukangana. Ndikufunanso kuti amayi azivala mwaulemu, modzilemekeza ndi moyenera. Adzikongoletse koma osati ndi tsitsi loluka mowonjeza muyeso kapena zokongoletsa zagolide kapena mikanda yamtengowapatali kapena ndi zovala zamtengowapatali. Koma adzikongoletse ndi ntchito zabwino zoyenera mayi wopembedza Mulungu. Amayi azikhala chete pophunzitsidwa ndi mtima ogonjera kwathunthu. Ine sindikulola kuti amayi aziphunzitsa kapena kulamulira amuna; koma akhale chete. Pakuti Adamu ndiye anayamba kupangidwa kenaka Hava. Ndipo Adamu si amene ananyengedwa koma mkazi ndiye amene ananyengedwa nachimwa. Ndipo mkazi adzapulumutsidwa pobereka mwana ngati apitiriza kukhala mʼchikhulupiriro, mʼchikondi ndi mʼkuyera mtima pamodzi ndi kudzichepetsa konse. Zowayenereza Oyangʼanira ndi Atumiki Mawu woona ndi awa: Ngati munthu akufunitsitsa atakhala woyangʼanira, ndiye kuti akufuna ntchito yabwino. Tsono woyangʼanira ayenera kukhala munthu wopanda chotsutsika nacho, mwamuna wa mkazi mmodzi yekha, woganiza bwino, wodziretsa, waulemu, wosamala bwino alendo, wodziwa kuphunzitsa. Asakhale chidakwa, asakhale wandewu, koma wofatsa, asakhale wokonda mikangano, kapena wokonda ndalama. Akhale wodziwa kusamala bwino banja lake ndi kulera ana ake bwino, kuti akhale omvera ndi aulemu weniweni. (Ngati munthu sadziwa kusamala banja lake lomwe, angathe bwanji kusamala mpingo wa Mulungu?) Asakhale wongotembenuka mtima kumene kuopa kuti angadzitukumule napezeka pa chilango monga Satana. Ayeneranso kukhala munthu wambiri yabwino ndi akunja, kuti anthu asamutonze nagwa mu msampha wa Satana. Momwemonso atumiki, akhale anthu oyenera ulemu, woona mtima, osakhala okonda zoledzeretsa, osakonda kupeza zinthu mwachinyengo. Ayenera kugwiritsa mozama choonadi cha chikhulupiriro ndi kukhala ndi chikumbumtima chabwino. Ayambe ayesedwa kaye, ndipo ngati palibe kanthu kowatsutsa, aloleni akhale atumiki. Momwemonso, akazi akhale olemekezeka, osasinjirira koma oganiza bwino ndi odalirika pa chilichonse. Mtumiki akhale wokhulupirika kwa mkazi wake ndipo ayenera kukhala wosamalira bwino ana ake ndi onse a pa khomo pake. Iwo amene atumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndipo amakhala chitsimikizo chachikulu cha chikhulupiriro chawo mwa Khristu Yesu. Cholinga cha Malangizo a Paulo Ngakhale ndili ndi chiyembekezo choti ndifika komweko posachedwapa, ndikukulemberani malangizo awa. Ine zina zikandichedwetsa kubwera, mudziwe za mmene anthu ayenera kukhalira mʼNyumba ya Mulungu, imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo, mzati ndi maziko achoonadi. Mosakayikira, chinsinsi cha chikhulupiriro chathu chachikulu: Khristu anaonekera ali ndi thupi la munthu, Mzimu anamuchitira umboni, angelo anamuona, analalikidwa pakati pa mitundu yonse, dziko lapansi linamukhulupirira, anatengedwa kupita kumwamba mwa ulemerero. Malangizo kwa Timoteyo Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda. Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto. Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika. Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero. Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata. Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu. Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo. Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu. Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira. Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa. Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja. Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera. Malangizo kwa Amayi Amasiye, Akulu Ampingo ndi Akapolo Usadzudzule munthu wachikulire mokalipa, koma umuchenjeze ngati abambo ako. Achinyamata uwatenge ngati abale ako. Amayi achikulire uwatenge ngati amayi ako ndipo amayi achitsikana uwatenge ngati alongo ako, nʼkuyera mtima konse. Uziwachitira ulemu akazi amasiye amene ali okhaokha. Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana ndi zidzukulu, anawo ayambe aphunzira kukwaniritsa udindo wawo pa banja lawo moopa Mulungu, potero akubweza zabwino kwa makolo awo ndi agogo awo. Pakuti zimenezi ndiye zimakondweretsa Mulungu. Mkazi wamasiye amene ali yekha ndi wopanda womuthandiza, ameneyo wayika chiyembekezo chake pa Mulungu, ndipo amapemphera kosalekeza usana ndi usiku kuti Mulungu azimuthandiza. Koma mkazi wamasiye amene amangokhalira kuchita zosangalatsa moyo wake, wafa kale ngakhale akanali ndi moyo. Pereka malangizo amenewa kwa anthu kuti akhale opanda zolakwa. Ngati wina sasamalira abale ake, makamaka a mʼbanja mwake mwenimweni, ameneyo wakana chikhulupiriro ndipo ndi woyipa kuposa wosakhulupirira. Mayi wamasiye aliyense amene sanakwanitse zaka 60 zakubadwa, asakhale mʼgulu la akazi amasiye. Akhale woti anakwatiwapo ndi mwamuna wake mmodzi yekha. Akhale mayi woti amadziwika bwino pa ntchito zake zabwino monga kulera ana, kusamalira alendo, kusambitsa mapazi a anthu a Mulungu, kuthandiza amene ali pa mavuto ndi kudzipereka pa ntchito zonse zabwino. Akazi amasiye achitsikana, usawayike mʼgulu limeneli. Pakuti zilakolako zawo zikayamba kuwavutitsa nʼkuwalekanitsa ndi Khristu, amafuna kukwatiwanso. Zikatero amadziweruza okha chifukwa aphwanya lonjezo lawo loyamba. Komanso amakhala ndi chizolowezi cha ulesi ndi kumangoyenda khomo ndi khomo. Ndipo sikungokhala aulesi kokha komanso kuchita miseche, kududukira za eni ake, kumangokamba zinthu zosayenera kukamba. Kotero, ndikulangiza akazi amasiye achitsikana kuti akwatiwe, akhale ndi ana, asamalire makomo awo ndipo asamupatse mdani mpata wonyoza Akazi amasiye ena apatuka kale nʼkumatsatira Satana. Ngati mayi aliyense wokhulupirira ali ndi akazi amasiye amene akuwasamalira, apitirizebe kuwasamalira ndipo asalemetse mpingo, kuti mpingo uthandize akazi amasiye amene ali okhaokha. Akulu ampingo amene amayangʼanira bwino zochitika za mu mpingo, ndi oyenera ulemu wowirikiza, makamaka amene ntchito yawo ndi kulalikira ndi kuphunzitsa. Pakuti Mawu a Mulungu amati, “Musamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha tirigu,” ndi “Wantchito ngoyenera kulandira malipiro ake.” Usamamvere mawu oneneza akulu ampingo pokhapokha patakhala mboni ziwiri kapena zitatu. Akulu ampingo amene akuchimwa, uwadzudzule poyera kuti ena aphunzirepo. Ndikukulamulira pamaso pa Mulungu, pamaso pa Yesu Khristu ndi pamaso pa angelo osankhika, kuti usunge malangizowa mosachotsera ndipo usachite kalikonse mokondera. Usafulumire kusanjika manja munthu, ndipo usavomerezane ndi anthu ena pa machimo. Usunge bwino kuyera mtima kwako. Uleke kumangomwa madzi okha, koma uzimwako vinyo pangʼono chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndi kudwala kwako kwa pafupipafupi. Anthu ena machimo awo amaonekeratu poyera, amakafika pa mpando wachiweruzo eni akewo asanakafike. Machimo a anthu ena amabwera mʼmbuyo mwawo. Momwemonso, ntchito zabwino zimaonekera poyera, ndipo ngakhale zipande kutero, sizingatheke kubisika. Onse amene ali mu ukapolo ayenera kuona ambuye awo ngati oyenera kuwachitira ulemu, kuti anthu anganyoze dzina la Mulungu ndi chiphunzitso chathu. Amene ambuye awo ndi okhulupirira, asawapeputse chifukwa ambuye ndi abale mʼchikhulupiriro. Mʼmalo mwake akuyenera kuwatumikira bwino chifukwa ambuye wawo ndi okondedwa monga okhulupirira ndiponso ndi odzipereka kusamalira akapolo awo. Aphunzitsi Onyenga ndi Kukonda Ndalama Zinthu izi ukuyenera kuziphunzitsa ndi kuwalamula anthu. Ngati wina aphunzitsa zosiyana ndi zimenezi, wosagwirizana ndi malangizo woona a Ambuye athu Yesu Khristu ndi chiphunzitso cholemekeza Mulungu, ameneyo ndi wodzitukumula ndipo sakudziwa chilichonse. Iyeyo ali ndi maganizo oyipa, wokonda kusemphana mawu ndi kutsutsana. Zimenezi zimabweretsa nsanje, mikangano, mʼnyozo, kuganizirana zoyipa, ndi kulimbana kosatha pakati pa anthu amitima yopotoka amene alandidwa choonadi ndipo amaganiza kuti kulemekeza Mulungu ndi njira yopezera chuma. Koma kulemekeza Mulungu kuli ndi phindu lalikulu. Pakuti sitinabweretse kanthu mʼdziko lapansi, ndipo sitingatengenso kanthu pochoka mʼdziko lapansi. Koma ngati tili ndi chakudya ndi zovala, zimenezi zitikwanire. Anthu amene amafuna kulemera amagwa mʼmayesero ndi mu msampha ndi mʼzilakolako zambiri zopusa ndi zoopsa zimene zimagwetsera anthu mʼchitayiko ndi mʼchiwonongeko. Pakuti kukonda ndalama ndiye muzu wa zoyipa za mitundu yonse. Anthu ena ofunitsitsa ndalama, asochera ndipo asiya njira yachikhulupiriro ndipo adzitengera zowawitsa zambiri. Malangizo Otsiriza kwa Timoteyo Koma iwe, munthu wa Mulungu, thawa zinthu zonsezi. Tsatira chilungamo, moyo wolemekeza Mulungu, chikhulupiriro, chikondi, kupirira ndi kufatsa. Menya nkhondo yabwino yachikhulupiriro. Gwiritsitsa moyo wosatha umene anakuyitanira pamene unavomereza bwino lomwe pamaso pa mboni zambiri. Ndikukulamula pamaso pa Mulungu amene amapatsa moyo zinthu zonse, ndiponso pamaso pa Khristu Yesu amene pochitira umboni pamaso pa Pontiyo Pilato, ananena zoona zenizeni. Usunge lamuloli mopanda banga ndi cholakwa kufikira Ambuye athu Yesu Khristu ataonekera. Pa nthawi yake Mulungu adzamubweretsa kwa ife. Mulungu ndi wodalitsika ndipo Iye yekha ndiye Wolamulira, Mfumu ya mafumu, Mbuye wa ambuye. Ndiye yekha wosafa ndipo amakhala mʼkuwala koopsa. Mulungu amene munthu aliyense sanamuone. Kwa Iye kukhale ulemu ndi mphamvu mpaka muyaya. Ameni. Za Kudalira Chuma Anthu onse amene ali ndi chuma uwalamule kuti asanyade kapena kuyika mitima yawo pa chuma chimene nʼchosadalirika. Koma chiyembekezo chawo chikhale mwa Mulungu amene amatipatsa mowolowamanja zonse zotisangalatsa. Uwalamule kuti azichita zabwino, kuti azikhala olemera pa ntchito zabwino, owolowamanja ndi okonda kugawana zinthu zawo ndi anzawo. Potero adzadziwunjikira chuma chokhalitsa ngati maziko okhazikika a nthawi zakutsogolo, kuti akalandire moyo, umene ndi moyo weniweni. Mawu Otsiriza Timoteyo, samalitsa zimene unapatsidwa. Upewe nkhani zopanda pake zosalemekeza Mulungu ndiponso maganizo otsutsana amene amaganizidwa molakwika kuti ndi nzeru. Anthu ena chifukwa chovomereza nzeru zotere, asochera nʼkutaya chikhulupiriro chawo. Chisomo chikhale nawe.