- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 1 ATESALONIKA Kalata Yoyamba ya Paulo Yolembera Atesalonika 1 Atesalonika 1 Ate KALATA YOYAMBA YA PAULO YOLEMBERA ATESALONIKA Paulo, Silivano ndi Timoteyo. Tikulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu. Chisomo ndi mtendere kwa inu. Kuyamikira Chikhulupiriro cha Atesalonika Ife timayamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu. Timakutchulani mʼmapemphero athu. Nthawi zonse timakumbukira ntchito yanu yachikhulupiriro, yachikondi ndi kupirira kwanu kwa chiyembekezo mwa Ambuye athu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu wathu ndi Atate. Abale okondedwa ndi Mulungu, tikudziwa kuti Mulungu anakusankhani, chifukwa uthenga wathu wabwino sunafike kwa inu ndi mawu okha, koma ndi mphamvu za Mzimu Woyera ndi chitsimikizo chachikulu. Mukudziwa mmene tinkakhalira pakati panu kuti tikuthandizeni. Inu mwakhala otitsatira athu ndi a Ambuye; ngakhale kuti panali masautso akulu, munalandira uthenga mwachimwemwe chochokera kwa Mzimu Woyera. Ndipo potero munakhala chitsanzo kwa abale onse a ku Makedoniya ndi Akaya. Kuchokera kwa inu, uthenga wa Ambuye unamveka ku Makedoniya ndi ku Akaya ndipo mbiri ya chikhulupiriro chanu mwa Mulungu yamveka ponseponse. Choncho sikofunikanso kuti tinene kanthu, pakuti iwo amafotokoza za momwe munatilandirira. Iwo amatiwuza za momwe munatembenukira kwa Mulungu kusiya mafano ndi kutumikira Mulungu wamoyo ndi woona. Ndipo mukudikira Mwana wake kuchokera kumwamba, Yesu, amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa. Iyeyo amatipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwera. Utumiki wa Paulo ku Atesalonika Abale, mukudziwa kuti kudzacheza kwathu kwa inu sikunali kosapindulitsa. Monga mukudziwa, ife nʼkuti titazunzika ndi kunyozedwa ku Filipi. Koma mothandizidwa ndi Mulungu wathu, tinalimba mtima mpaka kukulalikirani uthenga wake wabwino ngakhale ambiri ankatsutsana nafe. Pakuti kulalikira kumene tikuchita, sitikuchita ndi maganizo olakwika kapena zolinga zoyipa, kapenanso kufuna kukunamizani. Koma timayankhula monga anthu ovomerezeka ndi Mulungu ndi osungitsidwa Uthenga Wabwino. Ife sitikufuna kukondweretsa anthu koma Mulungu, amene amasanthula mitima yathu. Monga mukudziwa kuti sitinagwiritse ntchito mawu oshashalika kapena mtima wofuna phindu, Mulungu ndiye mboni yathu. Ife sitinafune kutamidwa ndi anthu, kapena ndi inu, kapena wina aliyense mwa inu. Ngati atumwi a Khristu tikanatha kukhala cholemetsa kwa inu, mʼmalo mwake tinali ngati ana aangʼono pakati panu. Monga mmene amayi amasamalira ana awo angʼono, moteronso tinakusamalirani. Chifukwa tinakukondani kwambiri, tinali okondwa kugawana nanu osati Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso miyoyo yathu. Abale, pakuti mukumbukira kugwira ntchito kwathu kwambiri ndi kuvutika; ife tinagwira ntchito usana ndi usiku ndi cholinga chakuti tisakhale cholemetsa, kwa aliyense pamene ife tinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu. Inu ndinu mboni, ndiponso Mulungu, kuti tinali oyera mtima, olungama ndi wopanda chifukwa pakati panu amene munakhulupirira. Monga mudziwa kuti ife tinkasamala aliyense wa inu monga abambo amasamalira ana ake, kulimbikitsa, kutonthoza ndi kukupemphani kuti mukhale moyo oyenera Mulungu amene anakuyitanani kuti mulowe mu ufumu wake ndi ulemerero. Ndipo ifenso tikuyamika Mulungu kosalekeza chifukwa mutalandira Mawu a Mulungu, amene munawamva kuchokera kwa ife, munawalandira osati ngati mawu a anthu, koma monga momwe alili, Mawu a Mulungu, amene akugwira ntchito mwa inu amene mukhulupirira. Pakuti inu abale, munakhala otsanzira mipingo ya Mulungu ya ku Yudeya, imene ili mwa Khristu Yesu. Munasautsidwa kuchokera kwa anthu a mtundu wanu, zinthu zomwezo zimene mipingo imeneyi inasautsidwa ndi Ayuda, amene anapha Ambuye Yesu ndi aneneri ndipo anatithamangitsanso ife. Iwo sakondweretsa Mulungu ndipo amadana ndi anthu onse ndikutiretsa ife kuti tisayankhule ndi a mitundu ina kuti angapulumuke. Motero iwo amadziwunjikira okha machimo awo. Mkwiyo wa Mulungu wa afikira tsopano. Paulo Afunitsitsa Kuonanso Atesalonika Koma abale, titasiyana kwa nthawi pangʼono (mʼthupi osati mʼmaganizo), tinayesetsa koposa kuti tikuoneni. Pakuti ife tinafuna kubweranso kwa inu, makamaka ine Paulo, ndinayesa kangapo koma Satana anatiletsa. Nanga chiyembekezo chathu, chimwemwe chathu kapena chaufumu chimene ife tidzanyadira pamaso pa Ambuye athu Yesu Khristu pamene abwere ndi chiyani? Kodi si inu? Indedi, inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe. Nʼchifukwa chake pamene sitinathenso kupirira, tinaganiza kuti kunali bwino kuti atisiye tokha ku Atene. Tinatuma Timoteyo, mʼbale wathu ndi mnzathu wogwira naye ntchito ya Mulungu yofalitsa Uthenga Wabwino wa Khristu, kuti adzakulimbitseni mitima ndi kukukhazikitsani mʼchikhulupiriro chanu, ndi cholinga chakuti wina asasunthike ndi mavutowa. Inu mukudziwa bwino lomwe kuti ndife oyenera kukumana ndi zimenezi. Kunena zoona, pamene tinali nanu, tinkakuwuzani kuti tidzayenera kuzunzidwa. Ndipo monga mukudziwa bwino, zimenezi zinachitikadi. Nʼchifukwa chake, pamene sindikanathanso kupirira, ndinatuma Timoteyo kuti adzaone mmene chikhulupiriro chanu chilili. Ndinkaopa kuti mwina wonyengayo, wakunyengani mʼnjira ina yake ndi kuti ntchito zathu zasanduka zosapindula. Nkhani Yolimbikitsa Kuchokera kwa Timoteyo Koma tsopano Timoteyo wabwera kuchokera kwanuko ndipo watibweretsera nkhani yabwino ya chikhulupiriro chanu ndi chikondi chanu. Iye watiwuzanso kuti masiku onse mumatikumbukira mokondwa, ndipo kuti mumafunitsitsa kutionanso, monga momwe ifenso timalakalakira kukuonani inuyo. Motero abale, mʼmasautso ndi mʼmazunzo athu onse, chikhulupiriro chanu chatilimbikitsa. Ife tsopano tili moyodi, pakuti mukuyima molimbika mwa Ambuye. Tingathe bwanji kuyamika Mulungu mokwanira poona chimwemwe chonse chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? Usana ndi usiku timapemphera ndi mtima wonse kuti tionanenso nanu, ndi kukwaniritsa zimene zikusowa pa chikhulupiriro chanu. Tikupempha kuti Mulungu ndi Atate athu mwini, ndi Ambuye athu Yesu, atikonzere njira yabwino kuti tidzafike kwanuko. Ambuye achulukitse chikondi chanu ndi kuti chisefukire kwa wina ndi mnzake ndiponso kwa wina aliyense, monga momwe chikondi chathu chichitira kwa inu. Iye alimbikitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera mtima pamaso pa Mulungu ndi Atate athu pamene Ambuye athu Yesu akubwera ndi oyera ake onse. Moyo Wokondweretsa Mulungu Potsiriza, abale, tinakulangizani kale momwe mukuyenera kukhalira kuti mukondweretse Mulungu, monga momwe mukukhaliramo. Tsopano tikukupemphani ndi kukulimbikitsani mwa Ambuye Yesu kuti muchite zimenezi koposa kale. Inu mukudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa ulamuliro wa Ambuye Yesu. Ndi chifuniro cha Mulungu kuti muyeretsedwe: kuti mupewe dama; aliyense wa inu aphunzire kulamulira thupi lake mʼnjira yoyera ndi yaulemu, osati yotsata chilakolako chonyansa monga amachitira akunja, amene sadziwa Mulungu. Pa zimenezi munthu asachimwire mʼbale wake kapena kumuonerera. Ambuye adzalanga anthu onse amene amachita machimo amenewa, monga tinakuwuzani kale ndi kukuchenjezani. Pakuti Mulungu sanatiyitane kuti tizichita zonyansa, koma kuti tikhale oyera mtima. Choncho, aliyense amene akukana malangizo awa sakukana munthu koma Mulungu, Mulungu weniweniyo amene amakupatsani Mzimu Woyera. Tsono kunena za kukondana wina ndi mnzake, nʼkosafunikira kuti tikulembereni, popeza ndi Mulungu amene anakuphunzitsani za kukondana wina ndi mnzake. Ndipo kunena zoona, mumakonda abale onse a mʼbanja la Mulungu a ku Makedoniya. Komabe, abale tikukulimbikitsani kuti muzichita zimenezi koposa kale. Yesetsani kuti mukhale moyo wofatsa. Aliyense asamale ntchito yakeyake ndi kugwira ntchito ndi manja ake. Mukatero akunja adzalemekeza makhalidwe anu a tsiku ndi tsiku, ndi kuti inuyo mukhale osadalira wina aliyense. Kubweranso kwa Ambuye Abale, ife sitikufuna mukhale osadziwa za amene akugona, kapena kumva chisoni ngati anthu ena opanda chiyembekezo. Ife timakhulupirira kuti Yesu anamwalira naukanso. Moteronso timakhulupirira kuti amene anamwalira ali mwa Yesu, Mulungu adzawaukitsa nʼkubwera nawo pamodzi ndi Yesuyo. Molingana ndi mawu a Ambuye mwini, tikukuwuzani kuti, ife amene tikanali ndi moyo, otsala mpaka kubwera kwa Ambuye, sitidzawasiya kumbuyo amene anagona kale. Pakuti Ambuye mwini adzatsika kuchokera kumwamba, ndi mfuwu waulamuliro, ndi liwu la mngelo wamkulu, ndi kulira kwa lipenga la Mulungu, ndipo akufa amene ali mwa Yesu adzauka poyamba. Kenaka, ife amene tili ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa pamodzi ndi iwo mʼmitambo kukakumana ndi Ambuye mlengalenga. Tsono ife tidzakhala ndi Ambuye mpaka muyaya. Nʼchifukwa chake tsono muzilimbikitsana ndi mawu amenewa. Tsiku la Ambuye Tsono abale, za nthawi ndi nyengo yake nʼkosafunikira kuti tikulembereni, chifukwa mukudziwa bwino lomwe kuti tsiku la Ambuye lidzafika ngati mbala usiku. Pamene anthu akunena kuti, “Mtendere ndi chitetezo,” chiwonongeko chidzafika pa iwo mwadzidzidzi, monga zowawa za amayi pobereka, ndipo sadzathawa. Koma inu abale, simuli mu mdima kuti tsiku limeneli lidzakudzidzimutseni ngati mbala. Nonse ndinu ana a kuwunika ndi ana a usana. Sindife anthu a usiku kapena mdima. Chomwecho tsono, tisafanane ndi ena amene akugona koma tikhale maso ndi odzisunga. Pakuti amene akugona, amagona usiku, ndi amene amaledzera, amaledzera usiku. Koma popeza ndife a usana, tikhale odzisunga, titavala chikhulupiriro ndi chikondi ngati chovala pachifuwa, ndi chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa. Pakuti Mulungu sanatisankhe kuti tikavutike ndi mkwiyo koma kuti tilandire chipulumutso kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iye anatifera ndi cholinga chakuti, kaya tili ndi moyo kapena tagona, tikhale naye pamodzi. Choncho limbikitsanani wina ndi mnzake ndi kuthandizana kukula mu mzimu, monga momwe mukuchitira. Malangizo Otsiriza Tsopano tikukupemphani abale kuti muziwalemekeza amene akugwira ntchito pakati panu, amene amakuyangʼanirani mwa Ambuye ndi amene amakulimbikitsani. Muziwachitira ulemu kwambiri mwachikondi chifukwa cha ntchito yawo. Mukhale pa mtendere wina ndi mnzake. Ndipo tikukupemphani abale, muwachenjeze amene akungokhala osagwira ntchito, alimbikitseni amanyazi, thandizani ofowoka ndipo muzilezera mtima aliyense. Onetsetsani kuti wina asabwezere choyipa kwa omuchitira choyipa koma nthawi zonse yesetsani kukhala okoma mtima kwa wina ndi mnzake; ndiponso ndi kwa anthu ena onse. Kondwerani nthawi zonse. Pempherani kosalekeza. Yamikani mu zonse, pakuti ichi ndi chifuniro cha Mulungu kwa inu mwa Khristu Yesu. Musazimitse moto wa Mzimu Woyera. Musanyoze mawu a uneneri. Yesani zinthu zonse. Gwiritsitsani chimene ndi chabwino. Mupewe choyipa cha mtundu wina uliwonse. Mulungu mwini, Mulungu wamtendere, akuyeretseni kotheratu. Mzimu wanu wonse, moyo ndi thupi zisungidwe zopanda cholakwa mpaka kubwera kwa Ambuye athu Yesu Khristu. Amene anakuyitanani ndi wokhulupirika ndipo Iye adzachita zimenezi. Abale, mutipempherere. Perekani moni wachikondi kwa onse. Pamaso pa Ambuye ndikulamula kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse. Chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu chikhale nanu.