- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 1 SAMUELI 1 Samueli 1 Samueli 1 Sam 1 Samueli Banja la Elikana Panali munthu wina wochokera ku Ramataimu, Mzofimu wa ku dziko la mapiri la Efereimu. Iyeyu dzina lake anali Elikana ndipo anali mwana wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu wa fuko la Efereimu. Iye anali ndi akazi awiri, Hana ndi Penina. Penina anali ndi ana, koma Hana analibe. Chaka ndi chaka Elikana ankachoka ku mudzi kwawo kupita ku Silo kukapembedza ndi kukapereka nsembe kwa Yehova Wamphamvuzonse. Ku Siloko kunali ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi amene anali ansembe a Yehova. Tsiku lopereka nsembe likafika Elikana amapereka magawo a nsembeyo kwa mkazi wake Penina ndi kwa ana ake onse aamuna ndi aakazi. Ngakhale ankamukonda Hana, koma ankamupatsa gawo limodzi popeza Yehova sanamupatse ana. Tsono popeza Yehova sanamupatse Hana ana, mkazi mnzakeyo ankamuyamba dala ndi cholinga chomukwiyitsa. Izi zimachitika chaka ndi chaka. Hana ankati akamapita ku Nyumba ya Yehova mkazi mnzakeyo ankamunyogodola. Choncho Hana ankangokhalira kulira osafuna ndi kudya komwe. Tsono mwamuna wake Elikana ankamufunsa kuti, “Hana ukulira chifukwa chiyani? Wakhumudwa ndi chiyani kuti sukufuna ndi kudya komwe? Kodi ine kwa iwe sindili woposa ana aamuna khumi?” Tsiku lina atatha kudya ndi kumwa ku Silo kuja, Hana anayimirira kukapemphera. Nthawiyi nʼkuti wansembe Eli atakhala pa mpando pa khomo la Nyumba ya Yehova. Hana anavutika mʼmoyo mwake, ndipo anapemphera kwa Yehova akulira kwambiri. Ndipo iye analumbira kuti, “Inu Yehova Wamphamvuzonse, ngati muyangʼana kusauka kwa mtumiki wanune, ndi kuyankha pemphero langa osandiyiwala ine mtumiki wanu pondipatsa mwana wamwamuna, ine ndidzamupereka mwanayo kwa inu Yehova masiku onse a moyo wake. Lumo silidzapita pa mutu pake.” Akupemphera choncho kwa Yehova, Eli ankamuyangʼana pakamwa. Hana ankapemphera chamumtima ndipo milomo yake inkangogwedera koma mawu ake samamveka. Choncho Eli anaganiza kuti anali ataledzera. Ndipo anamufunsa Hana kuti, “Kodi mukhala chiledzerere mpaka liti? Pitani, ayambe wakuchokani vinyo mwamwayo.” Koma Hana anayankha kuti, “Sichoncho mbuye wanga. Ndakhala ndikumukhuthulira Yehova chisoni changa. Sindinamwe vinyo kapena chakumwa choledzeretsa chilichonse, popeza nthawi yonseyi ndakhala ndikupereka kwa Yehova nkhawa yayikulu ndi mavuto anga. Musaganize kuti mtumiki wanu ndi kukhala mkazi wachabechabe. Ine ndakhala ndi kupereka nkhawa yanga yayikulu ndi zowawa zanga.” Eli anayankha, “Pitani mu mtendere, ndipo Mulungu wa Israeli akupatseni zimene mwamupemphazo.” Hana anati, “Mundikomerebe mtima mtumiki wanune.” Kenaka anachoka nakadya, ndipo sanaonekenso wachisoni. Elikana ndi banja lake anadzuka mmawa mwake nakapemphera pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anabwerera kwawo ku Rama. Elikana anakhala pamodzi ndi mkazi wake, ndipo Yehova anamukumbuka Hanayo. Motero Hana anakhala ndi pakati ndipo anabereka mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Samueli, popeza anati, “Ndinachita kumupempha kwa Yehova.” Hana Apereka Samueli kwa Yehova Elikana ndi banja lake lonse anapita kukapereka nsembe ya pa chaka kwa Yehova ndi kukakwaniritsa malonjezo ake. Koma Hana sanapite nawo popeza anawuza mwamuna wake kuti, “Mwanayu akadzaleka kuyamwa, ndidzapita naye ndi kukamupereka pamaso pa Yehova ndipo adzakhala kumeneko moyo wake wonse.” Elikana mwamuna wake anamuwuza kuti, “Chita chimene chakukomera. Tsala kuno mpaka utamusiyitsa kuyamwa, Yehova yekha akwaniritse mawu ake.” Choncho mkaziyo anatsala ku nyumba ndi kusamalira mwana wake mpaka atamuletsa kuyamwa. Atamuletsa kuyamwa, Hana anatenga mwanayo ali wachichepere, ndikupita naye ku nyumba ya Yehova ku Silo. Anatenga ngʼombe yamphongo ya zaka zitatu, ufa wa makilogalamu khumi, ndi thumba lachikopa la vinyo. Tsono anapha ngʼombe yamphongo ija ndi kupereka mwana uja kwa Eli. Ndipo Hana anati kwa Eli, “Mbuye wanga, ine ndikunenetsadi pamaso panu kuti ndine mkazi uja amene anayima pamaso panu ndi kumapemphera kwa Yehova. Ndinapempha mwana uyu, ndipo Yehova wandipatsa chimene ndinamupempha. Ndiye tsopano ine ndikumupereka kwa Yehova. Pa moyo wake wonse adzakhala wa Yehova.” Ndipo onse anapembedza Yehova kumeneko. Pemphero la Hana Ndipo Hana anapemphera nati, “Moyo wanga ukukondwera mwa Yehova; Ndiyenda mwa tukumutukumu chifukwa cha Yehova. Pakamwa panga pakula ndi kuseka adani anga mowanyogodola. Ndikukondwa chifukwa mwandipulumutsa. “Palibe wina woyera ngati Yehova, palibe wina koma inu nokha, palibe thanthwe lofanana ndi Mulungu wathu. “Musandiyankhulenso modzitama, pakamwa panu pasatuluke zonyada, pakuti Yehova ndi Mulungu wanzeru, ndipo ndiye amene amayesa ntchito za anthu onse. “Mauta a anthu ankhondo athyoka koma anthu ofowoka avala dzilimbe. Amene kale anali okhuta tsopano akukagula chakudya, koma iwo amene anali ndi njala sakumvanso njala. Amene anali wosabereka, wabereka ana aamuna asanu ndi awiri, koma iye wobereka ana ambiri watsala yekha. “Yehova amabweretsa imfa ndipo amaperekanso moyo, amatsitsira ku manda ndipo amawatulutsakonso. Yehova amasaukitsa ndipo amalemeretsa, amatsitsa ndipo amakweza. Iye amakweza osauka kuwachotsa pa fumbi, ndipo amachotsa anthu osowa pa dzala. Iye amawakhazika pamodzi ndi ana a mafumu, amawapatsa mpando waulemu. “Pakuti nsanamira za dziko lapansi ndi za Yehova, anakhazika dziko lapansi pa nsanamirazo. Iye adzateteza moyo wa anthu okhulupirika koma anthu oyipa adzawonongedwa mu mdima. “Pakuti munthu sapambana ndi mphamvu zake. Yehova adzaphwanya omutsutsa. Adzawaopsa ndi bingu kuchokera kumwamba; Yehova adzaweruza mathero a dziko lapansi. “Koma adzapereka mphamvu kwa mfumu yake, adzakuza mphamvu za odzozedwa wake.” Tsono Elikana anapita ku mudzi kwawo ku Rama, koma mnyamatayo amatumikira Yehova pansi pa ulamuliro wa wansembe Eli. Kuyipa kwa Ana a Eli Ana a Eli anali ana achabechabe pakuti samasamala za Yehova. Ndipo chizolowezi cha ansembe pakati pa anthu chinali motere kuti pamene munthu aliyense ankapereka nsembe ndipo nyama ija ikuwira pa moto, mtumiki wa wansembe ankabwera ndi chifoloko cha mano atatu mʼdzanja lake. Iye ankachipisa mu mʼphikamo, ndipo wansembeyo amatenga chilichonse chimene folokoyo yabaya. Umu ndi mmene ansembewo amachitira ndi Aisraeli onse amene amabwera ku Silo. Ndipo ngakhale mafuta asanatenthedwe, mtumiki wansembe amabwera ndi kunena kwa munthu amene akupereka nsembeyo kuti, “Ndipatse nyama kuti ndiwotche, pakuti Yehova salandira nyama yophika koma yayiwisi.” Ngati munthuyo anena kuti, “Apseretu mafuta poyamba, ndipo kenaka mutenge mmene mufunira,” mtumikiyo amayankha kuti, “Ayi ndipatse tsopano lino. Ngati sutero, ine nditenga molanda.” Tchimo la ana a Eli linali lalikulu kwambiri pamaso pa Yehova pakuti iwo amanyoza nsembe za Yehova. Koma Samueli amatumikira pamaso pa Yehova atavala efodi ya nsalu yofewa yosalala. Chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo ndi kukamupatsa akamapita ndi mwamuna wake kukapereka nsembe za pa chaka. Tsono Eli amadalitsa Elikana ndi mkazi wake ndi mawu akuti “Yehova akupatseni ana mwa mkazi uyu kulowa mʼmalo mwa amene anapempha ndi kumupereka kwa Yehova.” Ndipo Yehova anamukomera mtima Hana. Anakhala ndi pathupi ndi kubereka ana aamuna atatu ndi ana aakazi awiri. Ndipo Samueli ankakula pamaso pa Yehova. Tsono Eli anakalamba kwambiri. Iye ankamva zonse zimene ana ake aamuna ankachitira Aisraeli onse, ndiponso kuti ankagona ndi akazi pa chipata cha tenti ya msonkhano. Choncho anawafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zotere? Ine ndikumva kuchokera kwa anthu onse za zoyipa zanuzo. Ayi, ana anga si mbiri yabwino imene ndikumva anthu a Mulungu akufalitsa. Ngati munthu alakwira munthu mnzake, mwina Mulungu adzamupepesera, koma ngati munthu achimwira Yehova adzamupepesera ndani?” Koma ana ake sanamvere kudzudzula kwa abambo awo, pakuti chinali cholinga cha Yehova kuti awaphe. Ndipo mnyamata Samueli anapitirira kukula mu msinkhu, ndipo ankapeza kuyanja pamaso pa Yehova ndi anthu. Uneneri Wotsutsa Banja la Eli Tsiku lina munthu wa Mulungu anabwera kwa Eli ndipo anamuwuza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi Ine sindinadziwulule ndekha kwa banja la kholo lako pamene iwo anali akapolo a Farao ku Igupto? Ndipo ndinamusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti akhale wansembe wanga ndi kuti azipita pa guwa langa la nsembe, kufukiza Lubani ndi kuvala efodi pamaso panga. Ndinapatsa banja la abambo ako gawo la nsembe zonse zopsereza zimene Aisraeli amapereka. Nʼchifukwa chiyani ukunyoza nsembe ndi zopereka zanga zimene ndinalamula? Nʼchifukwa chiyani ukupereka ulemu kwa ana ako kuposa Ine podzinenepetsa nokha ndi zopereka zabwino kwambiri za nsembe zimene Aisraeli amapereka?’ ” “Paja Ine Yehova Mulungu wa Israeli ‘Ndinalonjeza kuti anthu a pa banja lako ndi a pa banja la abambo ako azidzanditumikira nthawi zonse.’ Koma tsopano ndikuti, ‘Zonsezi zithe!’ Tsopano anthu amene amandilemekeza Inenso ndidzawalemekeza koma iwo amene amandinyoza Ine ndidzawanyoza. Nthawi ikubwera imene ndidzachotsa anyamata ako ndi anyamata a pa banja la abambo ako, kotero kuti sipadzakhala munthu wokalamba pa banja lako. Pa mavuto ako udzayangʼana ndi maso ansanje zabwino zimene ndidzachitira Aisraeli ena. Mʼbanja lako simudzapezeka munthu wokalamba. Komabe pa banja lako mmodzi yekha ndidzamuleka wosamuchotsa kuti azidzanditumikira. Iyeyu azidzakuliritsa ndi kukumvetsa chisoni. Koma ena onse pa banja lako adzafa akanali aangʼono.” “ ‘Ndipo chimene chidzachitike kwa ana ako awiriwa, Hofini ndi Finehasi, chidzakhala chizindikiro kwa iwe. Onse awiri adzafa pa tsiku limodzi. Pambuyo pake ndidzasankha wansembe wokhulupirika, amene adzachita zimene zili mu mtima ndi mʼmaganizo mwanga. Ndidzakhazikitsa banja lako kolimba ndipo adzatumikira pamaso pa wodzozedwa wanga nthawi zonse. Ndipo aliyense wotsala wa banja lako adzabwera ndi kugwada pamaso pake kupempha ndalama kapena chakudya.’ Adzati, ‘Chonde ndiloleni kuti ndizithandizako pa ntchito iliyonse ya unsembe kuti ndipeze chakudya.’ ” Yehova Ayitana Samueli Samueli ankatumikira Yehova moyangʼaniridwa ndi Eli. Masiku amenewo mawu a Yehova sankamveka pafupipafupi. Kuona zinthu mʼmasomphenya sikunkachitikanso kawirikawiri. Tsiku lina Eli, amene maso anali ofowoka ndi kuti sankatha kuona bwino, anagona pa malo ake. Nthawiyi nʼkuti nyale ya Mulungu isanazimitsidwe. Samueli anali gone mu Nyumba ya Yehova, kumene kunali Bokosi la Chipangano cha Mulungu. Yehova anayitana Samueli. Iye anayankha kuti, “Wawa.” Ndipo iyeyo anathamangira kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera ndamva kuyitana.” Koma Eli anati, “Ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” Ndipo iye anapita kukagona. Yehova anayitananso, “Samueli!” Ndipo Samueli anadzuka ndi kupita kwa Eli nati, “Ndabwera popeza ndamva mukundiyitana.” Eli nati, “Mwana wanga, ine sindinakuyitane, bwerera kagone.” Nthawiyi nʼkuti Samueli asanadziwe Yehova ndipo Mawu a Yehova nʼkuti asanawululidwe kwa iye. Yehova anayitananso Samueli kachitatu ndipo Samueli anadzuka ndikupita kwa Eli ndipo anati, “Ndabwera popeza mwandiyitana ndithu.” Apo Eli anazindikira kuti Yehova ndiye ankayitana mnyamatayo. Tsono Eli anamuwuza Samueli kuti, “Pita ukagone ndipo akakuyitananso ukanene kuti, ‘Yankhulani Yehova, pakuti mtumiki wanu ndikumvetsera.’ ” Choncho Samueli anapita ndi kukagona pamalo pake. Yehova anabwera ndi kuyima pomwepo, ndi kuyitana monga nthawi zina zija, “Samueli! Samueli!” Ndipo Samueli anayankha, “Yankhulani, pakuti mtumiki wanu akumvetsera.” Ndipo Yehova anati kwa Samueli, “Taona, patsala pangʼono kuti ndichite chinthu china mu Israeli chimene chidzadabwitsa aliyense amene adzamve. Tsiku limenelo ndidzachitadi zonse zimene ndinayankhula zokhudza banja la Eli kuyambira poyamba mpaka pomaliza. Pakuti ndinamudziwitsa kuti Ine ndikhoza kulanga banja lake kwamuyaya chifukwa cha zoyipa zimene ana ake ankadziyipitsa nazo. Iye ankadziwa zimenezi koma osawaletsa. Nʼchifukwa chake ndinalumbira kuti, ‘Zoyipa zimene banja la Eli linandichita sizidzafafanizidwa mpaka muyaya ngakhale adzapereke nsembe kapena zopereka zina.’ ” Samueli anagona mpaka mmawa. Atadzuka anatsekula zitseko za Nyumba ya Yehova. Iye anachita mantha kumuwuza Eli za masomphenya ake. Koma Eli anamuyitana nati, “Samueli mwana wanga.” Samueli anayankha kuti, “Wawa.” Tsono Eli anafunsa kuti, “Yehova wakuwuza chiyani? Usandibisire. Mulungu akulange ndithu ngati undibisira chilichonse cha zimene wakuwuza.” Choncho Samueli anamuwuza zonse, sanamubisire kalikonse. Ndipo Eli anati, “Iye ndi Yehova, mulekeni achite chimene chamukomera.” Yehova anali ndi Samueli pamene amakula, ndipo zonse zimene ankayankhula zinkachitikadi. Ndipo Aisraeli onse kuyambira ku dera la Dani mpaka ku Beeriseba anazindikira kuti Yehova analozadi chala pa Samueli kuti akhale mneneri wake. Yehova anapitiriza kuoneka ku Silo, ndipo kumeneko anadziwulula yekha kwa Samueli mwa mawu ake. Ndipo mawu a Samueli anafika kwa Aisraeli onse. Afilisti Alanda Bokosi la Chipangano Aisraeli anapita kukamenya nkhondo ndi Afilisti. Aisraeli anamanga misasa yawo ku Ebenezeri, ndipo Afilisti anamanga ku Afeki. Afilisti anandanda kuyangʼana Aisraeli nayamba kumenyana. Nkhondo inakula ndipo Afilisti anagonjetsa Aisraeli napha anthu 4,000 pa malo a nkhondopo. Asilikali atabwerera ku misasa, akuluakulu a Israeli anafunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani Yehova walola kuti tigonjetsedwe lero pamaso pa Afilisti? Tiyeni tikatenge Bokosi la Chipangano cha Yehova ku Silo kuti Yehovayo abwere kukhala pakati pathu ndi kutipulumutsa mʼmanja mwa adani athu.” Choncho anatuma anthu ku Silo ndipo anakatenga Bokosi la Chipangano cha Yehova Wamphamvuzonse amene amakhala pa akerubi. Ndipo ana awiri a Eli, Hofini ndi Finehasi anatsagana nalo Bokosi la Chipangano cha Mulungu. Bokosi la Chipangano cha Yehova litafika ku msasa, Aisraeli onse anafuwula kwambiri mpaka nthaka inagwedezeka. Atamva kufuwulaku, Afilisti anafunsa, “Kodi kufuwula kwakukulu kumeneku ku misasa ya Ahebri ndi kwachiyani?” Atamva kuti Bokosi la Yehova lafika ku msasako, Afilisti anachita mantha pakuti iwo ankanena kuti, “Milungu yafika ku msasa. Iwo anati, ‘Tili pamavuto. Chinthu choterechi sichinachitikepo nʼkale lomwe. Atsoka ife! Adzatipulumutsa ndani mʼmanja mwa milungu yamphamvuyi? Iyi ndi milungu imene inakantha Aigupto ndi miliri yosiyanasiyana mʼchipululu. Limbani mtima Afilisti! Chitani chamuna, kuti mungakhale akapolo a Ahebri monga iwowa alili akapolo anu. Chitani chamuna ndipo menyani nkhondo!’ ” Choncho Afilisti anamenya nkhondo, ndipo anagonjetsa Aisraeli. Iwo anathawa aliyense kwawo. Ankhondo a Aisraeli oyenda pansi okwanira 30,000 anaphedwa. Ndipo Bokosi la Chipangano la Yehova linalandidwa, ndiponso ana awiri Eli, Hofini ndi Finehasi anaphedwa. Imfa ya Eli Tsiku lomwelo munthu wina wa fuko la Benjamini anathawa ku nkhondo ndipo anafika ku Silo. Iyeyu zovala zake zinali zongʼamba ndipo anadzithira dothi kumutu kuonetsa chisoni. Atafika, anapeza Eli atakhala pa mpando wake mʼmbali mwa msewu, akungoyangʼana, pakuti ankadera nkhawa Bokosi la Mulungu. Munthuyo atalowa mu mzindamo ndi kufotokoza zimene zinachitika ku nkhondo, anthu onse a mu mzindamo anayamba kulira. Eli atamva kulirako anafunsa kuti, “Kodi phokosoli likutanthauza chiyani?” Tsono munthu wa fuko la Benjamini uja anapita msanga kwa Eli kukamufotokozera. Nthawiyo nʼkuti Eli ali wa zaka 98 ndipo maso ake anali atachita khungu kotero kuti samatha kuona. Munthuyo anamuwuza Eli kuti, “Ine ndabwera kuchokera ku nkhondo, ndathawako lero lomwe lino.” Eli anafunsa, “Nanga nkhondo yayenda bwanji mwana wanga?” Iye anayankha kuti, “Aisraeli athawa pamaso pa Afilisti. Anthu ambirimbiri aphedwa. Ana anunso Hofini ndi Finehasi aphedwa. Bokosi la Mulungu nalonso lalandidwa.” Atangotchula Bokosi la Yehova, Eli anagwa chagada, kuchoka pa mpando wake umene unali mʼmbali mwa chitseko cha mpanda. Khosi lake linathyoka ndipo anafa, pakuti anali okalamba ndi onenepa kwambiri. Iye anatsogolera Israeli zaka makumi anayi. Nthawiyo, mpongozi wa Eli, mkazi wa Finehasi anali woyembekezera ndipo anali pafupi kuchira. Atamva kuti Bokosi la Mulungu lalandidwa ndi kuti mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake amwalira, ululu wa pobereka mwana unamufikira modzidzimutsa ndipo anabereka mwana. Popeza mkaziyo anali pafupi kumwalira, akazi amene amamuthandiza anati, “Usaope, wabereka mwana wamwamuna” Koma iye sanayankhe kapena kulabadirako. Tsono iye anatcha mwanayo dzina loti Ikabodi kutanthauza kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli,” chifukwa cha kulandidwa Bokosi la Mulungu ndi imfa ya mpongozi wake Eli ndi mwamuna wake. Ananena momwemo kuti, “Ulemerero wachoka mu Israeli, pakuti Bokosi la Mulungu lalandidwa.” Bokosi la Chipangano Pakati pa Afilisti Afilisti atalanda Bokosi la Mulungu lija, analitenga kuchoka ku Ebenezeri kupita ku Asidodi. Kenaka anatenga Bokosi la Chipanganolo nabwera nalo ku nyumba ya Dagoni ndi kuliyika pambali pa Dagoni. Anthu a ku Asidodi atadzuka mmawa mwake, anangoona Dagoni atagwa pansi chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova! Iwo anatenga Dagoni ndi kumuyimika pamalo pake. Koma mmawa mwakenso atadzuka, anaona Dagoni atagwa chafufumimba pamaso pa Bokosi la Yehova. Mutu wake ndi manja ake zinali zitaduka ndi kugwera pa khonde polowera, thunthu lake lokha ndilo linatsala. Nʼchifukwa chake mpaka lero ansembe a Dagoni kapena wina aliyense amene amalowa mʼkachisi wa Dagoni ku Asidodi saponda pa khonde. Yehova analanga koopsa anthu a ku Asidodi. Yehova anawawononga ndi kuwazunza ndi zithupsa Asidoniwa pamodzi ndi anthu a madera ozungulira. Anthu a ku Asidodi ataona zimene zimachitika anati, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lisakhale kuno chifukwa akutizunza ife pamodzi ndi mulungu wathu Dagoni.” Choncho anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anawafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu wa Israeli tichite nalo chiyani?” Iwo anayankha kuti, “Bokosi la Mulungu wa Israeli lipite ku Gati.” Kotero analichotsa Bokosi la Mulungu wa Israelilo. Koma atafika nalo ku Gati, Yehova analanga mzindawo, ndipo anthu anachita mantha aakulu. Iye anazunza anthu a mu mzindawo, ana ndi akulu omwe, ndi zithupsa. Choncho anatumiza Bokosi la Mulungu ku Ekroni. Koma Bokosi la Mulungu lija litangofika ku Ekroni, anthu a ku Ekroni analira kuti, “Abwera nalo Bokosi la Mulungu wa Israeli kwa ife kuti atiphe pamodzi ndi anthu athu.” Kotero iwo anayitana atsogoleri onse a Afilisti kuti asonkhane ndipo anati, “Chotsani Bokosi la Mulungu wa Israeli, libwerere ku malo ake. Tikapanda kutero lidzatipha ife ndi anthu athu.” Pakuti mu mzinda monse munali mantha aakulu kwambiri ndipo Mulungu ankawalanga kwambiri anthu a kumeneko. Anthu amene sanafe anavutika ndi zithupsa, ndipo kulira kwa anthu a mu mzindamo kunamveka kumwamba. Bokosi la Chipangano Libwerera ku Israeli Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, “Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake.” Iwo anayankha kuti, “Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani.” Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?” Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu. Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu. Nʼchifukwa chiyani mukuwumitsa mitima monga anachita Aigupto ndi Farao? Mulungu atawalanga anthu a ku Igupto aja kodi suja anawalola Aisraeli kuti azipita ndipo anapitadi? “Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu. Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita. Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.” Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola. Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa. Ngʼombe zija zinapita molunjika kutsata msewu wopita ku Beti Semesi zikulira njira yonse. Sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Akalonga a Afilisti anazitsatira mpaka mʼmalire a Beti-Semesi. Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa. Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova. Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova. Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo. Zifanizo zagolide za zithupsa zimene Afilisti anatumiza ngati nsembe zopepesera machimo kwa Yehova zinkayimirira mizinda isanu iyi motere: chimodzi cha ku Asidodi, china cha ku Gaza ndi zina za ku Asikeloni, Gati ndi Ekroni. Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero. Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri. Tsono anthu a ku Beti-Semesi anafunsa, “Ndani angathe kuyima pamaso pa Yehova Mulungu Woyera? Bokosi la Chipanganoli lipita kuti likachoka pano?” Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.” Choncho anthu a ku Kiriati-Yearimu anabwera ndi kudzatenga Bokosi la Yehova. Iwo anapita nalo ku nyumba ya Abinadabu ya ku phiri ndipo anapatula Eliezara mwana wake kuti aziyangʼanira Bokosi la Yehovalo. Samueli Agonjetsa Afilisti ku Mizipa Zaka makumi awiri zinapita kuyambira pamene Bokosi la Yehova linakhala ku Kiriati-Yearimu, ndipo anthu a Israeli onse analira kupempha Yehova kuti awathandize. Ndipo Samueli anati kwa nyumba yonse ya Israeli, “Ngati mukubwerera kwa Yehova ndi mtima wanu wonse, muchotse milungu yachilendo ndi Asiteroti pakati panu ndipo mitima yanu ikhazikike pa Yehova ndi kutumikira Iye yekha. Mukatero Iye adzakupulumutsani mʼmanja mwa Afilisti.” Choncho Aisraeli anachotsa milungu yawo ya Baala ndi Asitoreti ndi kutumikira Yehova yekha. Kenaka Samueli anati, “Sonkhanitsani Aisraeli onse ku Mizipa ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.” Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa. Afilisti anamva kuti Aisraeli asonkhana ku Mizipa, choncho akalonga awo anabwera kudzawathira nkhondo. Ndipo Aisraeli atamva anachita mantha chifukwa cha Afilisti. Choncho anati kwa Samueli, “Musasiye kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti atipulumutse mʼdzanja la Afilistiwa.” Ndipo Samueli anatenga mwana wankhosa wamkazi woyamwa ndi kumupereka monga nsembe yopsereza kwa Yehova. Iye anapemphera kwa Yehova mʼmalo mwa Aisraeli, ndipo Yehova anamuyankha. Samueli akupereka nsembe yopsereza, Afilisti anayandikira kuti ayambe kuwathira nkhondo Aisraeli. Koma tsiku limenelo Yehova anawaopseza Afilisti aja ndi mawu aakulu ngati bingu. Choncho anasokonezeka motero kuti Aisraeli anawagonjetsa. Aisraeli anatuluka ku Mizipa kuthamangitsa Afilisti aja nʼkumawapha mʼnjira yonse mpaka kumunsi kwa Beti-Kari. Kenaka Samueli anatenga mwala nawuyika pakati pa Mizipa ndi Seni. Iye anawutcha Ebenezeri, popeza anati, “Yehova watithandiza mpaka pano.” Kotero Afilisti anagonjetsedwa ndipo sanadzalowenso mʼdziko la Israeli. Yehova analimbana ndi Afilisti masiku onse a Samueli. Mizinda yonse imene Afilisti analanda kuchokera ku Ekroni mpaka ku Gati inabwezedwa kwa Aisraeli. Choncho Aisraeli anapulumutsa dziko lawo. Ndipo panalinso mtendere pakati pa Aisraeli ndi Aamori. Samueli anatsogolera Aisraeli moyo wake wonse. Chaka ndi chaka Samueli ankakonza ulendo wozungulira kuchokera ku Beteli mpaka ku Giligala ndi Mizipa, kuweruza milandu ya Aisraeli mʼmadera onsewa. Koma pambuyo pake ankabwerera ku Rama, kumene kunali nyumba yake. Ankaweruza Aisraeli kumeneko. Ndipo iye anamanga guwa lansembe la Yehova kumeneko. Aisraeli Apempha kuti Akhale ndi Mfumu Samueli atakalamba anasankha ana ake kuti akhale oweruza Aisraeli. Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya, ndipo ankaweruza ku Beeriseba. Koma ana akewo sanatengere makhalidwe ake abwino. Iwo ankapotokera ku zoyipa namatsata phindu mwachinyengo. Ankalandira ziphuphu ndi kumaweruza mwachinyengo. Tsono akuluakulu onse a Israeli anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Samueli ku Rama. Iwo anati kwa iye “Taonani, inu mwakula tsopano ndipo ana anu sakutsata makhalidwe anu abwino. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga momwe ikuchitira mitundu ina yonseyi.” Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova. Yehova anamuyankha nati, “Mvera zonse zimene anthuwa akukuwuza. Si ndiwe amene akumukana, koma akukana Ine kuti ndikhale mfumu yawo. Kuyambira tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mpaka lero zochita zawo zakhala zondikana Ine nʼkumatumikira milungu ina. Tsopano akukukananso iwe. Tsono amvere zimene akunena, koma uwachenjeze kwambiri ndipo uwawuzitse za khalidwe la mfumu imene idzawalamulire.” Samueli anawawuza anthu amene amamupempha mfumu aja mawu onse a Yehova. Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo. Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. Iyo idzatenga ana anu akazi kuti akhale oyenga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi kupanga buledi. Idzatenga minda yanu yabwino ya mpesa ndi ya mitengo ya olivi ndipo adzayipereka kwa antchito ake. Idzatenga gawo lakhumi la tirigu wanu ndi mphesa zanu ndi kupereka kwa nduna zake ndi akapitawo ake. Mfumuyo idzatenga antchito anu aamuna ndi aakazi. Idzatenganso ngʼombe zanu zabwino ndi abulu anu nʼkumazingwiritsa ntchito. Iyo idzatenga gawo lakhumi la zoweta zanu, ndipo inu eni mudzakhala akapolo ake. Nthawi imeneyo ikadzafika inu mudzalira momvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhira, koma Yehova sadzakuyankhani.” Koma anthu anakana kumumvera Samueli. Iwo anati, “Ayi! Ife tikufuna mfumu yotilamulira. Kotero ifenso tidzakhala ngati mayiko ena. Mfumu yathu idzatiweruza ndiponso idzatuluka nafe kutitsogolera kukamenya nkhondo.” Samueli atamva zonse zimene anthuwo ananena, iye anakazifotokozanso kwa Yehova. Yehova anamuyankha nati, “Amvere zimene akunena ndipo apatse mfumu.” Ndipo Samueli anati kwa Aisraeli aja, “Bwererani aliyense kwawo.” Samueli Adzoza Sauli Panali munthu wina wa fuko la Benjamini, wotchuka, dzina lake Kisi, mwana wa Abieli, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya. Iyeyu anali ndi mwana dzina lake Sauli, mnyamata wa maonekedwe abwino. Pakati pa Aisraeli onse panalibe wofanana naye. Anali wamtali kotero kuti anthu onse ankamulekeza mʼmapewa. Tsono abulu a Kisi, abambo ake a Sauli anasowa. Choncho Kisi anati kwa mwana wake Sauli, “Tenga wantchito mmodzi ndipo mupite mukafunefune abuluwo.” Choncho iwo anadutsa dziko la mapiri a Efereimu ndi dera la Salisa, koma sanawapeze. Anadutsa ku Saalimu koma abuluwo sanawapeze. Kenaka anadutsa dziko la Benjamini, koma osawapezabe. Atafika ku dera la Zufi, Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Tiye tibwerere, mwina abambo anga angasiye kudandaula za abulu ndipo adzayamba kudandaula za ife.” Koma mnyamatayo anayankha kuti, “Taonani, mu mzinda uwo muli munthu wa Mulungu. Anthu amamupatsa ulemu kwambiri, ndipo zonse zimene amanena zimachitika. Tiyeni tipite kumeneko tsopano. Mwina adzatiwuza kumene tiyenera kulowera.” Sauli anafunsa mnyamata wake kuti, “Tikapita tikamupatsa chiyani munthuyo pakuti chakudya chimene chinali mʼmatumba mwathu chatha? Tilibe mphatso iliyonse yoti timutengere munthu wa Mulungu. Nanga tili ndi chiyani?” Mnyamatayo anayankha kuti, “Onani, ndili ndi kandalama kakangʼono ka siliva. Ndikamupatsa munthu wa Mulunguyo ndipo akatidziwitsa kumene kuli abuluwo.” (Kale mu Israeli ngati munthu afuna kukapempha nzeru kwa Mulungu ankanena kuti, “Tiyeni tipite kwa mlosi.” Ndiye kuti munthu amene lero akutchedwa mneneri, kale ankatchedwa mlosi). Tsono Sauli anawuza mnyamata wake kuti, “Chabwino, tiye tipite.” Ndipo ananyamuka kupita ku mzinda umene kunali munthu wa Mulunguyo. Akukwera phiri kupita ku mzindawo anakumana ndi atsikana akutuluka mu mzindamo kukatunga madzi, ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mlosi uja alipo?” Iwo anayankha, “Inde alipo. Ali kutsogolo kwanuku, fulumirani tsopano, wangobwera kumene mu mzinda wathu uno lero, chifukwa lero anthu akupereka nsembe ku phiri. Mukangolowa mu mzindawo mumupeza asanapite ku phiri kukadya. Anthu sangayambe kudya iye asanabwere chifukwa iyeyu ayenera kudalitsa nsembeyo. Kenaka anthu oyitanidwa adzayamba kudya. Pitani tsopano, chifukwa muyenera kumupeza nthawi ino.” Choncho anapita ku mzinda kuja. Akulowa mu mzindamo, anaona Samueli akutuluka mu mzindamo akubwera kumene kunali iwo, koma amapita ku phiri, ku malo wopatulika. Koma chadzulo lake Sauli asanafike, Yehova anali atamuwuza kale Samueli za zimenezi kuti, “Mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini. Udzamudzoze kuti akhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Iye adzawapulumutsa mʼdzanja la Afilisti. Ine ndaona kuzunzika kwawo ndipo ndamva kulira kwawo.” Samueli atamuona Sauli, Yehova anamuwuza kuti, “Munthu ndinakuwuza uja ndi uyu. Iyeyu adzalamulira anthu anga.” Tsono Sauli anayandikira Samueli pa chipata ndipo anamufunsa, “Kodi mungandiwuze kumene kuli nyumba ya mlosi?” Samueli anayankha, “Ine ndine mlosiyo. Tsogolani kupita ku phiri pakuti lero mudya ndi ine, ndipo mawa mmawa ndidzakuwuzani zonse zimene zili mu mtima mwanu. Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?” Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?” Ndipo Samueli anatenga Sauli ndi mnyamata wake uja ndi kulowa nawo mʼchipinda chachikulu ndipo anawakhazika kutsogolo kwa anthu oyitanidwa. Onse pamodzi analipo anthu makumi atatu. Tsono Samueli anati kwa wophika, “Bwera nayo nyama imene ndinakupatsa, imene ndinakuwuza kuti uyisunge pambali.” Kotero wophikayo anatenga mwendo wa nyama ndipo anawuyika patsogolo pa Sauli. Samueli anati “Nayi nyama imene ndinakusungira kuti pa nthawi yake udye pamodzi ndi anthu amene ndawayitana.” Ndipo Sauli anadya tsiku limenelo ndi Samueli. Atatsika kuchoka ku phiri kuja, Samueli anamukonzera Sauli malo ogona pa denga la nyumba yake, ndipo Sauli anagona pamenepo. Tsono mʼbandakucha Samueli anayitana Sauli pa dengapo nati, “Konzeka ndipo ine ndikuperekeza.” Choncho Sauli anadzuka ndipo onse awiri, Samueli ndi Sauli anakalowa mu msewu. Atakafika ku mathero a mzindawo, Samueli anati kwa Sauli, “Muwuzeni mnyamata wanu kuti atsogole, koma inuyo muyime pangʼono kuti ndikuwuzeni mawu ochokera kwa Mulungu.” Ndipo Samueli anatenga botolo la mafuta nathira mafutawo pa mutu wa Sauli ndipo anapsompsona nati, “Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake, Aisraeli. Iwe udzalamulira anthu a Yehova ndiponso udzawapulumutsa mʼmanja mwa adani awo owazungulira. Chizindikiro chakuti Yehova wakudzoza kuti ukhale mtsogoleri wa anthu ake ndi ichi: Ukachoka pano lero lino, udzakumana ndi amuna awiri kufupi ndi manda a Rakele ku Zeliza mʼmalire mwa dziko la Benjamini ndipo adzakuwuza kuti, ‘Abulu amene munkafunafuna aja apezeka. Ndipo tsopano abambo ako asiya kuganiza za abulu ndipo akudera nkhawa za iwe.’ Iwo akufunsa kuti, ‘Kodi ndidzachita chiyani mmene mwana wanga sakuoneka?’ ” “Ndipo udzapyola pamenepo ndi kufika ku mtengo wa thundu wa ku Tabori. Kumeneko udzakumana ndi anthu atatu akupita kukapereka nsembe ku Nyumba ya Mulungu ku Beteli. Mmodzi adzakhala atanyamula ana ambuzi atatu, wina atanyamula malofu atatu a buledi, ndi winayo atanyamula thumba la vinyo. Adzakupatsa moni ndi kukupatsa malofu awiri a buledi. Iwe udzalandire bulediyo. “Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera. Kenaka Mzimu wa Yehova udzabwera pa iwe ndi mphamvu, ndipo udzayamba kulosera nawo pamodzi. Ndipo udzasinthika kukhala munthu wina. Zizindikiro izi zikakachitika, dzachite chilichonse manja ako angathe kuchita, pakuti Mulungu ali nawe. “Tsono tsogola kupita ku Giligala. Ine ndidzabwera ndithu kudzapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Koma ukandidikire masiku asanu ndi awiri mpaka ine nditabwera kuti ndidzakuwuze zomwe udzachite.” Sauli Avekedwa Ufumu Sauli akutembenuka kusiyana ndi Samueli, Mulungu anasintha mtima wa Sauli, ndipo zinthu zonsezi zinakwaniritsidwa tsiku lomwelo. Atafika ku Gibeya, anakumana ndi gulu la aneneri. Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwamphamvu, nayamba kulosa nawo. Pamene onse amene ankamudziwa kale anamuona akulosera pamodzi ndi aneneri, anafunsana wina ndi mnzake. “Kodi nʼchiyani chachitika ndi mwana wa Kisi? Kodi Sauli alinso mʼgulu la aneneri?” Munthu wina wa kumeneko anayankha kuti, “Nanga enawa abambo awo ndani?” Kotero kunayambika mwambi wakuti, “Kodi Saulinso ali mʼgulu la aneneri?” Sauli atasiya kuloserako, anapita ku kachisi ku phiri. Tsono amalume ake a Sauli anamufunsa ndi mnyamata wake kuti, “Munapita kuti?” Iye anayakha, “Timakafunafuna abulu koma titaona kuti sakupezeka, tinapita kwa Samueli.” Amalume ake a Sauli anati, “Chonde, ndifotokozereniko zimene Samueli wakuwuzani.” Sauli anati, “Iye anatitsimikizira kuti abulu anapezeka.” Koma sanawawuze amalume akewo za nkhani ija ya ufumu imene Samueli anamuwuza. Samueli anayitana Aisraeli onse kuti asonkhane pamaso pa Yehova ku Mizipa. Ndipo anawuza Aisraeli onse kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi kukupulumutsani mʼdzanja la Igupto ndi mʼdzanja la mafumu onse amene ankakuzunzani.’ Koma lero mwamukana Mulungu wanu amene amakupulumutsani mʼmavuto anu onse ndi mʼzowawa zanu. Ndipo mukuti, ‘Ayi, koma mutipatse mfumu yotilamulira.’ Tsopanotu sonkhanani pamaso pa Yehova mwa mafuko ndi mabanja anu.” Samueli atasonkhanitsa mafuko onse a Israeli, fuko la Benjamini linasankhidwa. Anasonkhanitsa fuko la Benjamini banja ndi banja. Pomaliza anasonkhanitsa banja la Matiri mmodzimmodzi ndipo Sauli mwana wa Kisi anasankhidwa. Koma atamufunafuna, sanamupeze. Tsono anthu anafunsanso kwa Yehova kuti, “Kodi munthuyu wabwera kale kuno?” Ndipo Yehova anayankha kuti, “Inde wabisala pakati pa katundu.” Iwo anathamanga ndi kukamutenga kumeneko. Atayimirira pakati pa anthu anapezeka kuti anali wamtali kuposa anthu ena mwakuti ankamulekeza mʼmapewa. Samueli anafunsa anthu onse kuti, “Kodi mukumuona munthu amene Yehova wasankha? Palibe wofanana naye pakati pa anthu onse.” Kenaka anthu onse anafuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!” Samueli anafotokozera anthu ntchito ndi udindo wa mfumu. Pambuyo pake analemba mʼbuku zonse zokhudza ntchito ndi udindo wa mfumu, ndipo bukulo analiyika pamaso pa Yehova. Kenaka Samueli analola aliyense kuti abwerere kupita kwawo. Sauli anapitanso ku mudzi kwawo ku Gibeya, pamodzi ndi anthu amphamvu amene Mulungu anawafewetsa mitima. Koma anthu ena achabechabe anati, “Kodi munthu uyu angathe bwanji kutipulumutsa?” Iwo anayamba kumunyoza Sauliyo, ndipo sankamupatsa ngakhale mphatso. Koma iye sanalabadireko. Sauli Apulumutsa Mzinda wa Yabesi Nahasi, Mwamoni anapita ndi kuzungulira mzinda wa Yabesi Giliyadi. Tsono anthu onse a ku Yabesi anapempha Nahasiyo kuti, “Muchite nafe pangano, ndipo tidzakutumikirani.” Koma Nahasi Mwamoni uja anayankha kuti, “Ndidzachita nanu pangano pokhapokha nditakolowola diso lakumanja la aliyense wa inu kuti ndichititse manyazi Aisraeli onse.” Akuluakulu a mzinda wa Yabesi anati kwa iye, “Utipatse masiku asanu ndi awiri kuti titumize uthenga mu Israeli monse. Ngati sipapezeka wodzatipulumutsa, ndiye ife tidzadzipereka kwa iwe.” Amithenga aja atafika kwawo kwa Sauli ku Gibeya ndi kufotokoza nkhaniyi kwa anthu onse, iwo analira motaya mtima. Pa nthawiyo nʼkuti Sauli akubwera kuchokera ku munda, ali pambuyo pa ngʼombe zake za ntchito ndipo anafunsa. “Nʼchiyani chawavuta anthuwa kuti azilira motere?” Ndipo anamufotokozera zomwe anthu a mu mzinda wa Yabesi ananena. Sauli atamva mawu awo, Mzimu wa Mulungu unabwera pa iye mwa mphamvu ndipo anakwiya kwambiri. Tsono anatenga ngʼombe ziwiri za ntchito, nazidula nthulinthuli. Ndipo anatumiza amithenga ndi nthulizo dziko lonse la Israeli ndi mawu akuti, “Umo ndi mmene adzachite ndi ngʼombe ya aliyense amene satsata Sauli ndi Samueli.” Ndipo anthu anachita mantha aakulu motero kuti onse ananyamuka ndi mtima umodzi. Pamenepo Sauli anawasonkhanitsa ku Bezeki nawawerenga, ndipo Aisraeli analipo 300,000, Ayuda analipo 30,000. Tsono Sauli anawuza amithenga ochokera ku Yabesi aja kuti, “Mukawawuze anthu a ku Yabesi Giliyadi kuti mawa nthawi ya masana adzapulumutsidwa.” Pamene amithengawo anapita ndi kukafotokoza nkhani imeneyi kwa anthu a ku Yabesi, iwo anasangalala kwambiri. Choncho anthu a ku Yabesi anawuza Nahasi kuti, “Mawa tidzadzipereka kwa inu ndipo inu mudzachite nafe chilichonse chokukomerani.” Tsono mmawa mwake Sauli anagawa anthuwo mʼmagulu atatu. Mmamawa kusanache iwo analowa mʼmisasa ya Aamoni ndi kuwapha mpaka masana. Amene anapulumuka anabalalika, aliyense kwakekwake. Sauli Avomerezedwa kukhala mfumu Kenaka anthu anafunsa Samueli kuti, “Kodi ndani aja ankanena kuti, ‘Kodi Sauli nʼkutilamulira ife?’ Bwera nawoni kuno kuti tidzawaphe.” Koma Sauli anati, “Palibe amene ati aphedwe lero, pakuti lero lino Yehova wagwira ntchito yopulumutsa Israeli.” Ndipo Samueli anati kwa anthuwo, “Tiyeni tipite ku Giligala kuti tikatsimikizenso kuti Sauli ndi mfumu yathu.” Choncho anthu onse anapita ku Giligala ndipo kumeneko Samueli anakalonga Sauli ufumu pamaso pa Yehova. Pambuyo pake anthu anapereka nsembe zachiyanjano pamaso pa Yehova, ndipo Sauli ndi Aisraeli onse anachita chikondwerero chachikulu. Samueli Atsanzika Anthu Pambuyo pake Samueli anawuza Aisraeli onse kuti, “Ine ndamvera zonse zimene munandiwuza ndipo ndakupatsani mfumu kuti izikulamulirani. Tsopano muli ndi mfumu imene izikutsogolerani, koma ine ndakalamba, kumutu kwanga kuli imvi zokhazokha ndipo ana anga ali pamodzi ndi inu. Ndakhala ndili mtsogoleri wanu kuyambira ndili mnyamata mpaka lero. Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.” Iwo anayankha kuti, “Inu simunatidyere masuku pamutu kapena kutizunza. Simunalande kanthu kalikonse ka munthu.” Samueli anawawuza kuti, “Yehova ndiye mboni pakati pa inu ndi ine, ndiponso wodzozedwa wake ndi mboni kuti lero simunapeze chilichonse mʼdzanja langa.” Iwo anati, “Inde, Yehova ndiye mboni.” Samueli anawawuzanso kuti, “Yehova ndiye amene anasankha Mose ndi Aaroni kuti atulutse makolo anu mʼdziko la Igupto. Nʼchifukwa chake tsopano imani pomwepa kuti ndikufotokozereni pamaso pa Yehova, za ntchito za chipulumutso zimene Yehova anachitira inu ndi makolo anu. “Yakobo atapita ku dziko la Igupto, Aiguptowo akuwazunza, iwo analirira kwa Yehova kuti awathandize, ndipo Yehova anatumiza Mose ndi Aaroni, amene anatulutsa makolo anu mʼdziko la Igupto ndi kudzawakhazika pa malo ano. “Koma iwo anayiwala Yehova Mulungu wawo, choncho Yehova anawapereka mʼdzanja la Sisera mkulu wa ankhondo wa mzinda wa Hazori, ndiponso mʼmanja mwa Afilisti ndi mfumu ya Mowabu. Mafumu onsewa anathira nkhondo makolo anu. Tsono iwo analira kwa Yehova nati, ‘Ife tachimwa, chifukwa tamusiya Yehova ndi kumatumikira mafano a Baala ndi Asiteroti. Koma tsopano tilanditseni mʼmanja mwa adani athu ndipo tidzakutumikirani.’ Choncho Yehova anatumiza Yeru-Baala, Bedani, Yefita ndi Samueli ndipo anakulanditsani mʼmanja mwa adani anu amene anakuzungulirani, kotero munakhala mwamtendere. “Koma mutaona kuti Nahasi mfumu ya Amoni inkabwera kudzamenyana nanu, inu munandiwuza kuti, ‘Ayi, ife tikufuna mfumu kuti itilamulire,’ ngakhale kuti Yehova Mulungu wanu ndiye anali mfumu yanu. Tsopano nayi mfumu imene mwayisankha, imene munayipempha. Onani, Yehova wakupatsani mfumu. Ngati muziopa Yehova ndi kumamutumikira ndi kumamumvera, osamupandukira ndiponso ngati inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzatsata Yehova Mulungu wanu, ndiye zinthu zonse zidzakuyenderani bwino. Koma mukapanda kumvera Yehova ndi kumupandukira, ndiye adzakulangani pamodzi ndi mfumu yanu yomwe. “Tsono imani pomwepa kuti muone chinthu chachikulu chimene Yehova ali pafupi kuchita pamaso panu! Kodi ino si nthawi yokolola tirigu? Komabe ndipemphera kwa Yehova kuti agwetse mvula ya mabingu. Zikatero mudzadziwa kuti tchimo lanu limene mwachita popempha mfumu kwa Yehova ndi lalikulu.” Choncho Samueli anapemphera, ndipo Yehova anatumiza mvula ya mabingu tsiku lomwelo. Apo anthu aja anaopa kwambiri Yehova ndi Samueli. Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.” Samueli anayankha kuti, “Musaope, inu mwachitadi tchimo ili, koma musaleke kumutsata Yehova ndi kumutumikira ndi mtima wanu wonse. Ndipo musatsate mafano achabechabe amene alibe phindu ndipo sangakupulumutseni popeza ndi achabechabe. Yehova adzakana anthu ake kuopa kuti dzina lake lamphamvu linganyozeke, pakuti chinamukondweretsa Yehova kuti akusandutseni inu kukhala anthu ake. Ndiponso kunena za ine, zisachitike kuti ndichimwire Yehova pakulephera kukupemphererani. Ndipo ine ndidzakuphunzitsani njira yabwino ndi yolungama kuti muziyendamo. Koma onetsetsani kuti mukuopa Yehova ndi kumutumikira mokhulupirika ndi mtima wanu wonse. Nthawi zonse muziganizira zinthu zazikulu wakhala akukuchitirani. Komabe mukapitirira kuchita zoyipa, ndiye kuti inu pamodzi ndi mfumu yanu mudzachotsedwa.” Samueli Adzudzula Sauli Sauli analowa ufumu ali ndi zaka makumi atatu, ndipo analamulira Israeli kwa zaka 42. Nthawi ina Sauli anasankha Aisraeli 3,000. Mwa iwowa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi ndi ku dziko la mapiri ku Beteli, ndipo 1,000 anali ndi Yonatani ku Gibeya ku Benjamini. Anthu ena onse otsala anawabweza kwawo. Yonatani anakantha mkulu wa ankhondo wa Afilisti ku Geba, ndipo Afilisti anamva kuti Aheberi awukira. Tsono Sauli anawuza amithenga kuti alize lipenga mʼdziko lonse la Israeli. Choncho Aisraeli onse anamva kuti Sauli wakantha mkulu wa ankhondo Wachifilisiti ndi kuti Afilisti anayipidwa nawo Aisraeli. Ndiye anthu anayitanidwa kuti abwere kwa Sauli ku Giligala. Tsono Afilisti anasonkhana kuti amenyane ndi Aisraeli. Iwo anali ndi magaleta 3,000, okwera pa akavalo 2,000 ndiponso asilikali kuchuluka kwake ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Iwo anapita ndi kukamanga misasa yawo ku Mikimasi, kummawa kwa Beti-Aveni. Pamene Aisraeli anaona kuti anali pamavuto akulu, poti anali atapanikizidwa kwambiri, anabisala mʼmapanga, mʼmaenje, mʼmatanthwe, mʼmakwalala ndi mʼzitsime. Ahebri ena anawoloka Yorodani mpaka kukafika ku dziko la Gadi ndi ku Giliyadi. Koma Sauli anakhalabe ku Giligala ndipo ankhondo onse amene anali naye anali njenjenje ndi mantha. Saulo anadikirira masiku asanu ndi awiri, monga mwa nthawi imene ananena Samueli. Koma Samueli sanabwere ku Giligala, ndipo anthu anayamba kumuthawa Sauli uja. Kotero iye anati, “Bwera nayoni nsembe yopsereza ndi nsembe ya chiyanjano.” Ndipo Sauli anapereka nsembe yopsereza. Atangomaliza kupereka nsembe, anangoona Samueli watulukira ndipo Sauli anapita kukamulonjera. Samueli anafunsa kuti, “Nʼchiyani chimene wachita?” Sauli anayankha kuti, “Nditaona kuti anthu ayamba kundithawa, ndi kuti inu simunabwere pa nthawi munanena ija, ndiponso kuti Afilisti akusonkhana ku Mikimasi, ndinati, ‘Tsopano Afilisti abwera kudzandithira nkhondo ku Giligala kuno, chonsecho sindinapemphe Yehova kuti andikomere mtima.’ Motero ndinakakamizika kupereka nsembe yopsereza.” Samueli anati, “Mwachita zopusa. Simunatsate zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muchite. Mukanazitsata, Yehova akanawukhazikitsa ufumu wanu mu Israeli mpaka kalekale. Koma tsopano ufumu wanu sudzakhalitsa. Yehova wapeza munthu wapamtima pake ndipo wamusankha kukhala mtsogoleri wa anthu ake chifukwa inu simunasunge malamulo a Yehova.” Kenaka Samueli anachoka ku Giligala ndi kupita ku Gibeyati ku dziko la Benjamini. Saulo anawerenga anthu amene anali naye ndipo analipo 600. Sauli Akonzekera Nkhondo Sauli ndi mwana wake Yonatani pamodzi ndi asilikali amene anali naye aja amakhala ku Geba ku dziko la Benjamini. Koma Afilisti anamanga misasa yawo ku Mikimasi. Ankhondo a Afilisti anatuluka mʼmisasa yawo mʼmagulu atatu. Gulu lina linapita ku Ofiri ku dziko la Suwala. Gulu lina linalunjika ku Beti-Horoni, ndipo gulu lachitatu linalunjika ku malire oyangʼanana ndi chigwa cha Zeboimu cha ku chipululu. Nthawi imeneyo nʼkuti mulibe osula zitsulo mʼdziko lonse la Israeli, pakuti Afilisti anati, “Tisawalole Aheberi kudzipangira okha malupanga kapena mikondo!” Kotero Aisraeli onse amapita kwa Afilisti kukanoletsa mapulawo, makasu, nkhwangwa ndi zikwakwa zawo. Mtengo wonolera mapulawo ndi makasu unali zigawo ziwiri za sekeli, mtengo wonolera zisonga ndi nkhwangwa unali gawo limodzi la Sekeli. Motero tsiku la nkhondolo panalibe lupanga kapena mkondo mʼdzanja la aliyense amene anatsatira Saulo ndi Yonatani. Koma Saulo ndi Yonatani, iwo okha ndiwo anali ndi zida. Yonatani Athira Nkhondo Afilisti Tsono gulu lina lankhondo la Chifilisti linapita kukalonda mpata wa Mikimasi. Tsiku lina Yonatani mwana wa Sauli anawuza mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka Afilisti tsidya ilo.” Koma iye sanawuze abambo ake. Sauli ankakhala mʼmalire a Gibeya pa tsinde pa mtengo wamakangadza ku Migironi. Anthu amene anali naye analipo 600. Pakati pawo panalinso Ahiya amene ankavala efodi. Iye anali mwana wa Ahitubi, mʼbale wake wa Ikabodi mwana wa Finehasi, mwana wa Eli, wansembe wa Yehova wa ku Silo. Koma palibe amene anadziwa kuti Yonatani wachoka. Pa mpata pamene Yonatani ankafuna kudutsa kukafika ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti kunali thanthwe lotsetsereka mbali ina ndi lina lotsetsereka mbali inayo. Thanthwe limodzi linkatchedwa Bozezi ndipo linalo linkatchedwa Seni. Thanthwe limodzi linali chakumpoto kuyangʼanana ndi Mikimasi, ndipo thanthwe linalo linali chakummwera kuyangʼanana ndi Geba. Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.” Mnyamata uja anati, “Chitani chilichonse chimene mtima wanu ukhumba. Ine ndili nanu pamodzi. Chimene mtima wanu ukhumba ndi chomwenso ine ndikhumba.” Yonatani anati, “Tiye tsono tiwoloke kupita kumene kuli anthuwo ndi kukadzionetsa kwa iwo. Akatiwuza kuti, ‘Imani pomwepo mpaka tikupezeni,’ ife tikangoyima pomwepo osapita kumene kuli iwoko. Koma akadzati, ‘Bwerani kuno,’ ndiye ife tikapitedi, chifukwa ichi chidzakhala chizindikiro chakuti Yehova wapereka mʼmanja mwathu.” Choncho awiriwa anadzionetsa ku kaboma ka nkhondo ka Afilisti. Tsono Afilistiwo anati, “Taonani! Aheberi akutuluka mʼmaenje mʼmene anabisala.” Anthu a ku kaboma kaja anafuwula kwa Yonatani ndi mnyamata wake uja kuti, “Bwerani kuno ndipo tikuphunzitsani phunziro.” Ndipo Yonatani anati kwa mnyamata wake. “Nditsate pakuti Yehova wapereka Afilistiwa mʼmanja mwa Aisraeli.” Choncho Yonatani anakwera mokwawa, ndipo mnyamata wake uja ankamutsata. Tsono Yonatani anathira nkhondo Afilisti aja namawagwetsa, ndipo mnyamata wake uja ankawapha pambuyo pa iyeyo. Nthawi yoyambayo Yonatani ndi mnyamata wake uja anapha anthu makumi awiri ndipo anawaphera pa malo ochepa okwanira ngati theka la ekala. Aisraeli Agonjetsa Afilisti Tsono gulu lonse la ankhondo, ndiye kuti iwo amene anali mʼmisasa ndi mʼminda ndiponso iwo amene anali ku kaboma ka ankhondo kaja, onse anagwidwa ndi mantha aakulu. Dzikonso linagwedezeka, choncho anthu anachita mantha koopsa. Alonda a Sauli a ku Gibeya dziko la Benjamini atangomwaza maso anangoona chigulu cha asilikali chikumwazikana uku ndi uku. Kenaka Sauli anawawuza anthu amene anali naye kuti, “Awerengeni asilikali kuti muona amene wachoka.” Atawawerenga anapeza kuti Yonatani ndi mnyamata wake womunyamulira zida zake za nkhondo palibe. Tsono Sauli anawuza Ahiya kuti, “Bwera nalo Bokosi la Mulungulo.” (Nthawi imeneyo nʼkuti efodiyo ili ndi Ahiya pamaso pa Aisraeli). Pamene Sauli amayankhula ndi wansembe, phokoso limanka likulirakulira mu msasa wa Afilisti, Kotero Sauli anati kwa wansembe, “Leka kuwombeza.” Ndipo Sauli ndi asilikali onse amene anali naye anasonkhana kupita kukamenya nkhondo, ndipo anangoona chisokonezo chachikulu kwambiri. Afilisti akuphana okhaokha. Aheberi ena amene kale anali ndi Afilisti mpaka kukakhala ku misasa yawo, iwonso anatembenuka nakhala pamodzi ndi Aisraeli amene ankatsata Sauli ndi Yonatani. Ngakhale Aisraeli amene ankabisala ku dziko lamapiri la Efereimu atamva kuti Afilisti akuthawa, nawonso anawathamangitsa Afilistiwo nawathira nkhondo. Nkhondo inapitirira mpaka kufika ku Beti-Aveni. Choncho Yehova anapulumutsa Aisraeli tsiku limenelo. Yonatani Adya Uchi Koma asilikali a Israeli anavutika tsiku limenelo, chifukwa Sauli anawalumbirira Aisraeli kuti, “Wotembereredwa munthu aliyense amene adzadya kusanade, ine ndisanalipsire adani anga!” Kotero palibe wankhondo aliyense amene analawa chakudya. Gulu lonse la ankhondo linalowa mʼnkhalango mmene munali uchi. Atalowa mʼnkhalango, anaona uchi ukukha, koma palibe amene anadya, pakuti ankaopa lumbiro lija. Koma Yonatani sanamve kuti abambo ake anawalumbirira anthu aja choncho anatenga ndodo yake imene inali mʼdzanja lake ndipo anayipisa mu chisa cha njuchi. Choncho iye anadya uchiwo ndipo mʼmaso mwake munayera. Kenaka mmodzi mwa Asilikali anamuwuza kuti, “Abambo ako alumbirira anthu nati, ‘Wotembereredwa munthu aliyense amene adye chakudya lero.’ Nʼchifukwa chake anthu alefuka.” Yonatani anati, “Abambo anga achita chinthu choyipira dziko. Taonani mʼmaso mwanga mwayera chifukwa ndalawa uchiwu pangʼono. Zikanakhala zabwino kwambiri anthuwa akanadya lero zofunkha za adani awo. Zikanatero tikanapha Afilisti ochuluka.” Tsiku limenelo Aisraeli anapha Afilisti kuchokera ku Mikimasi mpaka ku Ayaloni. Koma Aisraeliwo analefuka kwambiri ndi njala. Choncho iwo anathamangira pa zofunkha ndipo anatenga nkhosa, ngʼombe ndi ana angʼombe. Iwo anazipha zonsezi nazidya pamodzi ndi magazi omwe. Koma anthu ena anawuza Sauli kuti, “Taona anthu akuchimwira Yehova pakudya nyama yomwe ili ndi magazi.” Ndipo Sauli anati, “Mwaonetsa kusakhulupirika. Tsopano gubuduzirani mwala waukulu pano.” Kenaka Sauli anati, “Mwazikanani pakati pa anthu ndi kukawawuza kuti aliyense abwere ndi ngʼombe yake kapena nkhosa yake, ndipo adzayiphe pomwe pano ndi kuyidya. Musachimwire Yehova pakudya nyama imene ili ndi magazi.” Kotero aliyense anabwera ndi ngʼombe yake usiku womwewo ndi kuyipha pomwepo. Ndipo Sauli anamangira Yehova guwa. Ili linali guwa loyamba limene Sauli anamangira Yehova. Sauli anati, “Tiyeni titsatire Afilisti usikuwu ndi kulanda zinthu zawo mpaka mmawa. Tisasiyepo wamoyo ndi mmodzi yemwe.” Ankhondowo anayankha kuti, “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.” Koma wansembe anati, “Tipemphe uphungu kwa Mulungu poyamba.” Choncho Sauli anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndiwatsatire Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwathu?” Koma Mulungu sanamuyankhe tsiku limenelo. Choncho Sauli anati, “Bwerani kuno nonse atsogoleri a anthu, ndipo tiyeni tione kuti kodi tchimo limeneli lachitika bwanji lero? Pali Yehova amene amapulumutsa Israeli, ngakhale tchimolo litapezeka ndi mwana wanga Yonatani, iye afe ndithu.” Koma palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthuwo amene anamuyankha. Tsono Sauli anawuza Aisraeli onse kuti, “Inu mukhale mbali imodzi. Ine ndi mwana wanga Yonatani tikhala mbali inayo.” “Chitani chilichonse chimene chikukomerani.” Ndipo Sauli anapemphera kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, “Chifukwa chiyani simunandiyankhe ine mtumiki wanu lero lino? Ngati tchimoli lipezeka ndi ine kapena ndi Yonatani mwana wanga, Inu Mulungu wa Israeli, aoneke ndi Urimu. Koma ngati wochimwa ndi anthu anu, Aisraeli aoneke Tamimu.” Maere anagwera Sauli ndi Yonatani ndipo anthu anapezeka osalakwa. Sauli anati, “Chitani maere pakati pa ine ndi Yonatani mwana wanga.” Ndipo maere anagwera Yonatani. Kenaka Sauli anati kwa Yonatani, “Ndiwuze chimene wachita.” Ndipo Yonatani anamuwuza kuti, “Ine ndinangolawa uchi pangʼono ndi ndodo yangayi. Ndiye ine ndili wokonzeka kufa.” Sauli anati, “Mulungu andilange ngakhale kufa kumene, ngati sufa iwe Yonatani.” Koma anthuwo anafunsa Saulo kuti, “Kodi Yonatani afe, iye amene wagwira ntchito iyi yayikulu yopulumutsa Aisraeli? Osatheka! Pali Yehova ngakhale tsitsi ndi limodzi lomwe lapamutu pake silidzathothoka, pakuti wachita zimenezi lero ndi thandizo la Mulungu.” Choncho anthuwo anamupulumutsa Yonatani, ndipo sanaphedwe. Pambuyo pake Sauli analeka kulondola Afilisti, kenaka anabwerera ku dziko lawo. Sauli ali mtsogoleri wa Israeli, anachita nkhondo ndi adani awa omuzungulira: Mowabu, Amoni, Edomu mafumu a ku Zoba ndi Afilisti. Kulikonse kumene ankapita ankawagonjetsa. Anachita nkhondo mwamphamvu ndi kugonjetsa Aamaleki. Choncho anapulumutsa Aisraeli mʼmanja mwa anthu amene ankawalanda zinthu zawo. Banja la Sauli Ana aamuna a Sauli anali Yonatani, Isivi ndi Maliki-Suwa. Analinso ndi ana aakazi awiri, dzina la mwana wake wamkulu wamkazi linali Merabi ndipo la mwana wake wamngʼono wamkazi linali Mikala. Dzina la mkazi wake linali Ahinoamu. Iyeyu anali mwana wa Ahimaazi. Dzina la mkulu wa ankhondo a Sauli linali Abineri mwana wa Neri, mʼbale wa abambo a Sauli. Kisi abambo a Sauli ndi Neri abambo a Abineri anali ana a Abieli. Pa moyo wake wonse, Sauli ankakhalira kuchita nkhondo pakati pa Israeli ndi Afilisti. Ndipo Sauli ankati akaona munthu aliyense wamphamvu kapena wolimba mtima ankamulemba ntchito mu gulu lake lankhondo. Yehova Akana Sauli Kukhala Mfumu Samueli anawuza Sauli kuti, “Yehova anandituma ine kuti ndikudzozeni kukhala mfumu ya anthu ake, Aisraeli. Tsopano imvani zimene Yehova akunena. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Ine ndidzalanga Aamaleki chifukwa cha zimene anawachita Aisraeli. Paja iwo analimbana ndi Aisraeli pa njira pamene Aisraeliwo ankachoka ku Igupto. Tsopano pita kathire nkhondo Aamaleki ndi kuwononga kwathunthu zinthu zonse zimene ali nazo. Musakasiyeko munthu ndi mmodzi yemwe. Mukaphe amuna ndi akazi, ana ndi makanda, ngʼombe ndi nkhosa, ngamira ndi abulu.’ ” Kotero Sauli anayitana ankhondo ake nawawerenga ku Telaimu. Ankhondo oyenda pansi analipo 200,000 ndipo mwa iwowa 10,000 anali a fuko la Yuda. Sauli anapita ku mzinda wa Aamaleki nawubisalira mʼkhwawa. Tsono Sauli anawuza Akeni kuti, “Samukani, muchoke pakati pa Aamaleki kuti ine ndisakuwonongeni pamodzi ndi iwo pakuti inu munaonetsa kukoma mtima kwa Aisraeli onse pamene ankatuluka mʼdziko la Igupto,” Choncho Akeni anachoka pakati pa Aamaleki. Tsono Sauli anakantha Aamaleki kuchokera ku Havila mpaka ku Suri, kummawa kwa Igupto. Sauli anatenga Agagi mfumu ya Aamaleki, koma anthu ake onse anawapha ndi lupanga. Koma Sauli ndi ankhondo ake sanaphe Agagi, sanaphenso nkhosa ndi ngʼombe zabwino ngakhalenso ana angʼombe ndi ana ankhosa onenepa. Chilichonse chimene chinali chabwino sanachiphe. Koma zonse zimene zinali zoyipa ndi zachabechabe anaziwononga. Kenaka Yehova anawuza Samueli kuti, “Ine ndikumva chisoni chifukwa ndinayika Sauli kukhala mfumu. Wabwerera mʼmbuyo, waleka kunditsata ndipo sanamvere malangizo anga.” Samueli anapsa mtima, ndipo analira kwa Yehova usiku wonse. Samueli anadzuka mmamawa ndipo anapita kukakumana ndi Sauli. Koma anthu anamuwuza kuti, “Sauli anabwera ku Karimeli, ndipo kumeneko wadziyimikira mwala wachikumbutso cha iye mwini. Tsopano wachokako ndipo wapita ku Giligala.” Samueli atamupeza Sauli, Sauliyo anati kwa Samueli, “Yehova akudalitseni! Ndachita zonse zimene Yehova analamula.” Koma Samueli anati, “Nanga bwanji ndikumva kulira kwa nkhosa ndi ngʼombe?” Sauli anayankha, “Zimenezi Asilikali azitenga kuchokera kwa Aamaleki. Iwo anasungako nkhosa ndi ngʼombe zabwino kuti akapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu, koma zina zonse anaziwononga.” Koma Samueli anati kwa Sauli, “Khala chete! Ima ndikuwuze zimene Yehova wandiwuza usiku wathawu.” Sauli anayankha kuti, “Ndiwuzeni.” Apo Samueli anati, “Munali wamngʼono pa maso pa anthu, koma tsopano mwasanduka mtsogoleri wa mafuko a Israeli. Yehova anakudzozani kuti mukhale mfumu yolamulira Aisraeli. Ndipo Yehova anakutumani kuti, ‘Pitani mukawononge kwathunthu Aamaleki, anthu oyipa aja. Mukachite nawo nkhondo mpaka kuwatheratu.’ Chifukwa chiyani simunamvere mawu a Yehova? Chifukwa chiyani munathamangira zofunkha ndi kuchita choyipira Yehova?” Koma Saulo anawuza Samueli kuti, “Ine ndinamveradi mawu a Yehova. Ndinapita kukachita zimene Yehova anandituma. Ndinabwera naye Agagi, mfumu ya Amaleki, koma Aamaleki ena onse anaphedwa. Koma pa zofunkhazo anthu anatengapo nkhosa, ngʼombe ndi zabwino zina zoyenera kuwonongedwa kuti akapereke ngati nsembe kwa Yehova Mulungu wanu ku Giligala.” Koma Samueli anayankha kuti, “Kodi Yehova amakondwera ndi nsembe zopsereza ndi nsembe zina kapena kumvera mawu a ake? Taona, kumvera ndi kwabwino kuposa nsembe, ndipo kutchera khutu ndi kwabwino kuposa kupereka mafuta a nkhosa. Pakuti kuwukira kuli ngati tchimo lowombeza, ndipo kukhala nkhutukumve kuli ngati tchimo lopembedza mafano. Chifukwa mwakana mawu a Yehova. Iyenso wakukana kuti iweyo ukhale mfumu.” Tsono Sauli anati kwa Samueli, “Ine ndachimwa. Ndaphwanya malamulo a Yehova ndiponso malangizo anu. Ndinkaopa anthu ndipo ndinawamvera. Tsopano ndikukupemphani, khululukireni tchimo langa ndipo mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova.” Koma Samueli anawuza Sauli kuti, “Ine sindibwerera nawe. Inu mwakana mawu a Yehova. Choncho Iyenso wakukanani kuti musakhale mfumu yolamulira Aisraeli.” Samueli akutembenuka kuti azipita, Sauli anagwira mpendero wa mkanjo wake, ndipo unangʼambika. Samueli anati kwa iye, “Yehova wangʼamba ufumu wanu kuchoka kwa inu, ndipo waupereka kwa mnzanu woposa inu. Mulungu wa ulemerero wa Israeli sanama kapena kusintha maganizo ake; pakuti iye si munthu, kuti asinthe maganizo ake.” Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.” Pamenepo Samueli anabwerera ndi Sauli, ndipo Sauli anapembedza Yehova. Kenaka Samueli anati, “Bwera nayeni kuno Agagi, mfumu ya Amaleki ija.” Choncho Agagi anapita kwa Samueli mokondwa chifukwa ankaganiza kuti, “Ndithu zowawa za imfa zapita.” Koma Samueli anati, “Monga momwe lupanga lako linasandutsira amayi kukhala wopanda ana, momwemonso amayi ako adzakhala opanda mwana pakati pa amayi.” Ndipo Samueli anapha Agagi pamaso pa Yehova ku Giligala. Ndipo Samueli anapita ku Rama, koma Sauli anapita ku mudzi kwawo ku Gibeya wa Sauli. Samueli sanamuonenso Sauli mpaka imfa yake ngakhale kuti ankamulira Sauliyo. Yehova anamva chisoni kuti anasankha Sauli kuti akhale mfumu ya Israeli. Samueli Adzoza Davide Kukhala Mfumu Yehova anati kwa Samueli, “Kodi udzamulira Sauli mpaka liti, popeza Ine ndamukana kuti akhale mfumu ya Israeli? Dzaza mafuta mʼbotolo lako ndipo unyamuke kupita kwa Yese wa ku Betelehemu popeza ndadzisankhira mmodzi mwa ana ake kukhala mfumu.” Koma Samueli anati, “Kodi ndingapite bwanji? Sauli akamva zimenezi adzandipha.” Yehova anayankha, “Tenga ngʼombe yayikazi ndipo ukanene kuti, ‘Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Ukamuyitane Yese ku mwambo wa nsembe, ndipo ine ndidzakuwuza choti ukachite. Ukandidzozere amene ndikakulozere.’ ” Samueli anachita zimene Yehova ananena, ndipo anabweradi ku Betelehemu kuja. Akuluakulu a mu mzindawo anamuchingamira ali njenjenje ndi mantha ndipo anamufunsa kuti, “Kodi mwabwera mwa mtendere?” Samueli anayankha kuti, “Inde, kwabwino. Ndabwera kudzapereka nsembe kwa Yehova. Mudzipatule ndipo mubwere kudzapereka nsembe pamodzi nane.” Kenaka iye anamupatula Yese ndi ana ake aamuna ndipo anawayitana kudzapereka nsembe. Pamene anafika, Samueli anaona Eliabu ndipo anaganiza “Ndithu wodzozedwa wa Yehova uja ndi uyu wayima pamaso pakeyu.” Koma Yehova anati kwa Samueli, “Usaone maonekedwe ake kapena msinkhu wake, pakuti ndamukana iyeyu. Yehova sapenya zimene munthu amapenya. Anthu amapenya zakunja, koma Mulungu amapenya za mu mtima.” Kenaka Yese anayitana Abinadabu namubweretsa pamaso pa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanamusankhenso ameneyu.” Ndipo Yese anayitana Sama, koma Samueli anati, “Ngakhale uyu Yehova sanamusankhe.” Pambuyo pake, Yese anayitana ana ake amuna asanu ndi awiri kuti apite kwa Samueli. Koma Samueli anati, “Yehova sanasankhe amenewa.” Tsono Samueli anafunsa Yese kuti, “Kodi awa ndi ana ako onse aamuna?” Yese anayankha kuti, “Ayi, alipo wina wamngʼono amene watsala, koma akuweta nkhosa.” Samueli anati, “Apite munthu akamutenge popeza sitipereka nsembe mpaka iye atabwera.” Choncho anatuma munthu kukamutenga ndipo anabwera naye. Iye anali wofiirira, wa maonekedwe abwino ochititsa kaso. Ndipo Yehova anati, “Mudzoze popeza ndi ameneyu.” Samueli anatenga botolo la mafuta ndi kumudzoza pamaso pa abale ake, ndipo Mzimu wa Yehova unabwera mwamphamvu pa Davide kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo. Pambuyo pake Samueli anabwerera ku Rama. Davide Atumikira Sauli Nthawi imeneyo Mzimu wa Yehova unamuchokera Sauli, ndipo mzimu woyipa wochokera kwa Yehova unayamba kumuzunza. Atumiki a Sauli anati, “Taonani mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu ukukuzunzani. Ndiyetu, inu mbuye wathu titumeni ife antchito anu kuti tikafune munthu wodziwa bwino kuyimba zeze. Tsono pamene mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu wakufikirani, iye azidzayimba ndipo mudzakhala bwino.” Choncho Sauli anati kwa atumiki ake, “Chabwino, kandipezereni munthu wodziwa bwino kuyimba ndipo mubwere naye kuno.” Mmodzi mwa antchito ake anati, “Ine ndinaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu. Ndiye munthu wodziwa bwino kuyimba, wolimba mtima, ngwazi pa nkhondo, wodziwa kuyankhula ndi wokongola. Ndipotu Yehova ali ndi iye.” Ndipo Sauli anatumiza amithenga kwa Yese kukanena kuti, “Nditumizireni mwana wanu Davide, amene amaweta nkhosa.” Choncho Yese anatenga bulu namunyamulitsa buledi, thumba la vinyo ndi mwana wambuzi mmodzi. Zonsezi anamupatsa mwana wake Davide kuti akapereke kwa Sauli. Davide anafika kwa Sauli ndipo anayamba ntchito. Sauli anamukonda kwambiri Davide ndipo anamusandutsa wonyamula zida zake za nkhondo. Kenaka Sauli anatumiza mawu kwa Yese ndi kuti, “Mulole kuti Davide azinditumikira, pakuti ndamukonda kwambiri.” Nthawi zonse mzimu woyipa wochokera kwa Mulungu umati ukamufikira Sauli, Davide ankatenga zeze wake nʼkumamuyimbira. Choncho Sauli ankapeza bwino, ndipo mzimu woyipa uja unkamusiya. Davide ndi Goliati Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo ku Soko mʼdziko la Yuda. Iwo anamanga misasa yawo ku Efesi-Damimu, pakati pa Soko ndi Azeka. Sauli ndi Aisraeli anasonkhana namanga misasa mʼchigwa cha Ela ndipo anandandalitsa ankhondo kuti amenyane ndi Afilisti. Afilisti anali phiri lina ndipo Aisraeli analinso phiri lina, ndipo pakati pawo panali chigwa. Tsono munthu wina wamphamvu, dzina lake Goliati wochokera ku Gati anatuluka ku misasa ya Afilisti. Msinkhu wake unali pafupipafupi mamita atatu. Iye ankavala chipewa chamkuwa ndi malaya achitsulo olemera makilogalamu 57. Ankavalanso zokuta miyendo yake zamkuwa, ndipo ankanyamula nthungo ya mkuwa pa phewa pake. Thunthu la mkondo wake linali ngati mkombero wowombera nsalu, ndipo mutu wa mkondowo unkalemera makilogalamu asanu ndi awiri. Patsogolo pake pamakhala munthu wonyamula zida zake za nkhondo. Goliatiyo anayimirira ndi kufuwula kwa ankhondo a Israeli, nati, “Nʼchifukwa chiyani mwakonzekera nkhondo chotere? Kodi sindine Mfilisiti ndipo inu sindinu akapolo a Sauli? Sankhani munthu kuti abwere kwa ine. Ngati angathe kumenyana nane ndi kundipha, ife tidzakhala akapolo anu, koma ngati ine ndimugonjetsa ndi kumupha, inu mudzakhala akapolo athu ndi kumatitumikira.” Ndipo Mfilisitiyo anati, “Bwerani lero timenyane basi! Patseni munthu kuti ndimenyane naye.” Atamva mawu a Mfilisitiyo, Sauli ndi Aisraeli onse anataya mtima nachita mantha kwambiri. Davide anali mwana wa munthu wa fuko la Efurati dzina lake Yese amene amachokera ku Betelehemu mʼdziko la Yuda. Yese anali ndi ana aamuna asanu ndi awiri. Pa nthawi ya Sauli nʼkuti ali wokalamba. Ana atatu oyamba kubadwa a Yese nʼkuti atapita nawo ku nkhondo pamodzi ndi Sauli. Woyamba dzina lake anali Eliabu, wachiwiri anali Abinadabu, ndipo wachitatu anali Sama. Davide ndiye anali mzime. Ana aakulu atatuwo ndiwo anapita ku nkhondo ndi Sauli. Koma Davide ankapita ku misasa ya Sauli ndi kubwerako kuti azikaweta nkhosa za abambo ake ku Betelehemu. Kwa masiku makumi anayi, Mfilisiti uja ankabwera mmawa ndi madzulo kumadzionetsera. Tsiku lina Yese anawuza mwana wake Davide kuti, “Atengere abale ako makilogalamu khumi a tirigu wokazinga ndi malofu a buledi khumi ndipo upite nazo mofulumira ku misasa yawo. Utengerenso wolamulira wa gulu lawo tchizi khumi uyu. Ukaone mmene abale ako akukhalira ndipo ubwere ndi kanthu kosonyeza kuti ali bwino. Sauli, abale akowo ndi asilikali onse a Israeli ali ku chigwa cha Ela, akumenyana ndi Afilisti.” Mʼmamawa mwake Davide anasiya nkhosa mʼmanja mwa munthu wina ndipo anatenga zakudyazo nanyamuka monga momwe Yese abambo ake anamulamulira. Anakafika ku misasa pamene asilikali ankapita kukandanda pa mzere ku nkhondo, nʼkufuwula mfuwu wankhondo. Aisraeli ndi Afilisti anandanda pa mzere wankhondo moyangʼanana. Tsono Davide anasiyira zakudya zija munthu wosunga katundu nathamangira kumene kunali ankhondo kuja ndi kukalonjera abale ake. Pamene iye ankayankhula nawo anangoona Goliati wa ku Gati uja akuchoka pa mzere wa Afilisti akufuwula mawu onyoza monga mwa masiku onse, ndipo Davide ankawamva. Aisraeli ataona munthuyo, anamuthawa ndi mantha aakulu. Ndipo Aisraeli ankanena kuti, “Kodi mwamuona munthu akubwerayo? Iye amangobwera kudzanyoza Israeli. Tsono mfumu inati kuti idzapereka chuma chambiri kwa munthu amene adzamuphe. Idzaperekanso mwana wake wamkazi kuti amukwatire ndiponso banja la abambo ake silidzaperekanso msonkho mu Israeli.” Davide anafunsa anthu amene anayima pafupi naye kuti, “Kodi adzamuchita chiyani munthu amene adzapha Mfilisiti uyu ndi kuchotsa chitonzo pakati pa Israeli? Mfilisiti wosachita mdulidweyu ndi ndani kuti azinyoza gulu lankhondo la Mulungu wamoyo?” Anthu anamuwuzanso zonse zimene mfumu inanena kuti idzachitira munthu amene adzapha Mfilisitiyo. Eliabu, mkulu wake wa Davide, atamumva akuyankhula ndi anthuwo, anamukwiyira ndipo anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani wabwera kuno? Ndipo wasiyira yani nkhosa zochepazo mʼchipululu? Ndikudziwa kuti ndiwe wodzikuza ndiponso woyipa mtima. Unabwera kuno kuti udzaonere nkhondo.” Davide anati, “Kodi ndachita chiyani ine? Kodi ndisamayankhule?” Ndipo anamuchokera napita kwa munthu wina ndipo anamufunsa nkhani yomweyo, ndipo anthu anamuyankha iye monga poyamba paja. Mawu amene Davide anayankhula atamveka, anthu anakafotokozera Sauli ndipo Sauli anamuyitanitsa. Davide anati kwa Sauli, “Munthu aliyense asataye mtima chifukwa cha Mfilisitiyu. Ine kapolo wanu ndipita kukamenyana naye.” Sauli anayankha Davide kuti, “Iwe sungathe kupita kukamenyana ndi Mfilisitiyu. Iwe ukanali mnyamata, koma iyeyu ndi amene wakhala akumenya nkhondo kuyambira unyamata wake.” Koma Davide anati kwa Sauli, “Kapolo wanune ndinkaweta nkhosa za abambo anga. Ndipo mkango kapena chimbalangondo chikamabwera ndi kugwira mwana wankhosa pakati pa nkhosazo, ine ndinkatsatira ndi kupha chirombocho. Choncho ndinkapulumutsa mwana wankhosa uja mʼkamwa mwake. Ndipo chinkati chikandiwukira, ine ndinkagwira tchowa lake, nʼkuchikantha mpaka kuchipha. Ine kapolo wanu ndinapha mkango ngakhalenso chimbalangondo. Tsono Mfilisiti wosachita mdulidweyu adzaphedwa monga zinazo chifukwa wanyoza ankhondo a Mulungu wamoyo. Yehova amene anandilanditsa mʼkamwa mwa mkango ndi chimbalangondo adzandilanditsa mʼmanja mwa Mfilisiti uyu.” Sauli anati kwa Davide, “Pita, ndipo Yehova akhale nawe.” Ndipo Sauli anamveka Davide mwinjiro wake. Anamuveka zovala zankhondo ndi chipewa cha mkuwa. Davide anamangirira lupanga pa mwinjirowo. Atayesa kuyenda nazo, analephera chifukwa anali asanazizolowere. Iye anati kwa Sauli, “Sindingathe kuyenda nazo chifukwa sindinazizolowere.” Ndipo anazivula. Pambuyo pake anatenga ndodo yake mʼmanja. Kenaka anasankha miyala yosalala bwino mu mtsinje ndi kuyiika mʼthumba lake la ku ubusa. Legeni ili mʼmanja mwake, Davide ananyamuka kukakumana ndi Mfilisiti uja. Tsono Mfilisiti uja anayambapo kupita kumene kunali Davide, mnyamata wonyamula zida zake za nkhondo ali patsogolo pake. Mfilisitiyo atangomuona Davide, anamunyoza popeza kuti Davide anali mnyamata chabe wofiirira ndi wa maonekedwe abwino. Iye anati kwa Davide, “Kodi ndine galu, kuti ubwere kwa ine ndi ndodo?” Ndipo Mfilisitiyo anamutemberera Davide potchula mayina a milungu yake. Iye anatinso, “Bwera kuno ndipo ndidzapereka mnofu wako kwa mbalame zamlengalenga ndi kwa zirombo zakuthengo!” Koma Davide anati kwa Mfilisitiyo, “Iwe wabwera kwa ine ndi lupanga, mkondo ndi nthungo, koma ine ndikubwera kwa iwe mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa ankhondo Aisraeli amene iwe ukuwanyoza. Anatinso lero lino Yehova adzakupereka mʼmanja mwanga. Ndidzakukantha ndi kudula mutu wako. Ndidzapereka mitembo ya asilikali a Afilisti kwa mbalame za mlengalenga, ndi kwa zirombo zakuthengo ndipo dziko lonse lapansi lidzadziwa kuti mu Israeli muli Mulungu. Onse amene asonkhana pano adzadziwa kuti Mulungu sapulumutsa anthu ndi lupanga kapena mkondo, pakuti nkhondo ndi ya Yehova. Iye adzakuperekani mʼmanja mwathu.” Mfilisitiyo akusendera pafupi kuti akumane naye, Davideyo anathamangira mofulumira ku mzere wa nkhondo kukakumana naye. Davideyo anapisa dzanja lake mʼthumba lake natengamo mwala ndipo anawuponya, nalasa pa mphumi pa Mfilisitiyo. Mwalawo unalowa pa chipumi chake, ndipo anagwa chafufumimba. Kotero Davide anamupambana Mfilisitiyo pomugenda ndi mwala wa legeni ndi kumupha. Mʼmanja mwa Davide munalibe lupanga. Davide anathamanga nakayimirira pamwamba pa Mfilisiti uja. Anasolola lupanga lake lomwe moyikamo mwake, namupha pomudula mutu wake. Afilisti ataona kuti ngwazi yawo yafa, anathawa. Ndipo Aisraeli ndi anthu a ku Yuda ananyamuka, ndipo akufuwula anathamangitsa Afilisti aja mpaka ku Gati ndi ku zipata za Ekroni. Anthu akufa awo amagwa njira yonse ya ku Saaraimu mpaka ku Gati ndi ku Ekroni. Aisraeli anabwerako kothamangitsa Afilisti kuja ndipo anadzatenga zonse zimene zinali mʼmisasa ya Afilistiwo. Pambuyo pake Davide anatenga mutu wa Mfilisitiyo napita nawo ku Yerusalemu, koma anayika zida za Mfilisitiyo mu tenti yake. Sauli ataona Davide akupita kukakumana ndi Mfilisitiyo anafunsa Abineri, mkulu wa ankhondo kuti, “Abineri, kodi mnyamatayu ndi mwana wa yani?” Abineri anayankha kuti, “Ndithu mfumu muli apa ine sindikumudziwa.” Mfumu inati, “Pita kafufuze kuti mnyamata ameneyu ndi mwana wa yani.” Davide atangobwerako kokapha Mfilisiti kuja, Abineri anamutenga nabwera naye kwa Sauli, mutu wa Mfilisiti uja uli mʼmanja mwake. Sauli anamufunsa, “Mnyamata iwe, kodi paja ndiwe mwana wayani?” Davide anati, “Ndine mwana wa mtumiki wanu Yese wa ku Betelehemu.” Sauli Achitira Nsanje Davide Davide atatha kuyankhula ndi Sauli, mtima wa Yonatani unagwirizana ndi mtima wa Davide, ndipo iye ankamukonda Davide monga momwe ankadzikondera yekha. Choncho Sauli anamusunga Davideyo kuyambira tsiku limenelo ndipo sanamulole kuti abwerere ku nyumba ya abambo ake. Ndipo Yonatani anapanga pangano ndi Davide chifukwa ankamukonda monga momwe ankadzikondera. Yonatani anavula mkanjo umene anavala ndipo anamupatsa Davide pamodzi ndi zovala za nkhondo, lupanga, uta ndi lamba. Davide ankapita kulikonse kumene Sauli ankamutuma kuti apite kukamenya nkhondo, ndipo ankapambana. Choncho Sauli anamupatsa udindo woyangʼanira gulu lankhondo. Ichi chinakondweretsa anthu onse ngakhalenso atsogoleri a nkhondo a Sauli. Anthu akubwerera kwawo Davide atapha Mfilisiti uja, amayi anatuluka mʼmizinda yonse ya Israeli, akuyimba ndi kuvina kukachingamira mfumu Sauli. Ankayimba ndi kuvina mokondwa, kwinaku ngʼoma ndi zitoliro zikulira. Amayiwo ankalandizana nyimbo mokondwera namati: “Sauli wapha 1,000, Koma Davide wapha miyandamiyanda.” Koma Sauli anapsa mtima kwambiri ndipo mawu amenewa anamuyipira. Iye anati, “Iwo amuwerengera Davide miyandamiyanda, koma ine 1,000 okha. Nanga chatsalanso nʼchiyani kuti atenge? Si ufumu basi?” Ndipo kuyambira tsiku limeneli Sauli ankamuchitira nsanje Davide. Mmawa mwake mzimu woyipa uja unabwera mwamphamvu pa Sauli. Sauli anayamba kubwebweta mʼnyumba mwake. Davide ankamuyimbira zeze monga nthawi zonse. Sauli anali ndi mkondo mʼdzanja lake. Tsono anawuponya mkondowo, namati mu mtima mwake, “Ndimubaya Davide ndi kumukhomera ku khoma.” Koma Davide anawulewa kawiri konse. Pambuyo pake Sauli amamuopa Davide chifukwa Yehova anali ndi Davideyo, nʼkumusiya Sauli. Kotero Sauli anamuchotsa Davide pamaso pake ndi kumuyika kukhala mtsogoleri wa ankhondo 1,000. Choncho Davide ankapita ndi kubwera akutsogolera ankhondowa. Davide ankapambana kwambiri pa chilichonse chimene amachita chifukwa Yehova anali naye. Sauli ataona momwe Davide ankapambanira, iye anamuopa kwambiri. Koma Aisraeli onse ndi anthu a Yuda ankamukonda Davide chifukwa ankawatsogolera pa nkhondo zawo. Tsiku lina Sauli anawuza Davide kuti, “Nayu Merabi mwana wanga wamkazi wamkulu. Ine ndakupatsa kuti umukwatire. Koma unditumikire molimba mtima pomenya nkhondo za Yehova.” Poteropo Sauli ankanena kuti, “Ndisamuphe ndi manja angawa koma aphedwe ndi Afilisti!” Ndipo Davide anati kwa Sauli, “Ine ndine yani, ndipo abale anga kapena banja la abambo anga ndife yani mʼdziko la Israeli kuti ndikhale mpongozi wa mfumu?” Koma pa nthawi yoti Merabi mwana wa Sauli akwatiwe ndi Davide, Sauli anamupereka kwa Adrieli wa ku Mehola kuti amukwatire. Koma Mikala mwana wamkazi wa Sauli anamukonda Davide ndipo Sauli atamva za zimenezi, anakondwera. Sauli ankaganiza kuti, “Ndimupatse amukwatire kuti akhale ngati msampha kwa Davideyo, ndipo adzaphedwe ndi Afilisti.” Choncho Sauli anawuza Davide kachiwiri, “Tsopano udzakhala mkamwini wanga.” Sauli analamulanso nduna zake kuti, “Muyankhuleni Davide mwamseri ndi kumuwuza kuti, ‘Taona, mfumu imakondwera nawe, ndipo nduna zake zonse zimakukonda. Tsono ukhale mkamwini wa mfumu.’ ” Iwo anakamuwuza Davide mawu amenewa, koma Davide anati, “Kodi inu mukuganiza kuti ndi chinthu chapafupi kukhala mpongozi wa mfumu? Ine ndine wosauka ndiponso wosatchuka.” Nduna za Sauli zinamuwuza zonse zimene anayankha Davide. Sauli anayankha kuti, “Kamuwuzeni Davide kuti, ‘Mfumu sikufuna malowolo a mtundu wina uliwonse koma timakungu ta msonga za mavalo a Afilisti 100 kuti ilipsire adani ake.’ ” Maganizo a Sauli anali akuti Davide aphedwe ndi Afilisti. Nduna za Saulizo zitamuwuza Davide zimenezi, anakondwera kuti akhale mpongozi wa mfumu. Koma nthawi imene anapatsidwa isanathe, Davide ndi anyamata ake anapita ndi kukapha Afilisti 200. Iye anabwera ndi timakungu tija natipereka tonse kwa mfumu kuti akhale mpongozi wa mfumu. Kotero Sauli anapereka mwana wake wamkazi, Mikala, kwa Davide kuti amukwatire. Sauli atazindikira kuti Yehova anali ndi Davide ndiponso kuti mwana wake Mikala amamukonda Davide, iye anapitirirabe kumuopa Davide ndi kumadana naye moyo wake wonse. Nthawi zonse pamene atsogoleri a Afilisti ankatuluka kukamenya nkhondo, Davide ankapambana kuposa nduna zonse za Sauli. Choncho dzina lake linatchuka kwambiri. Sauli Ayesanso Kupha Davide Sauli anawuza mwana wake Yonatani ndi nduna zake zonse kuti aphe Davide. Koma Yonatani amamukonda kwambiri Davide. Choncho anawuza Davide kuti, “Abambo anga Sauli akufuna kukupha. Tsono uchenjere. Mmawa upite ukabisale ndipo ukakhale komweko. Ine ndidzapita ndi kukayima pafupi ndi abambo anga ku munda kumene iwe ukabisale. Ndipo ndidzayankhula ndi abambo anga za iwe ndipo chilichonse chimene ndikamve ndidzakuwuza.” Tsono Yonatani anakanena zabwino za Davide kwa abambo ake Sauli ndipo anati, “Mfumu musachimwire mtumiki wanu Davide, sanakuchimwireni, koma amakuchitirani zabwino kwambiri. Iye anayika moyo wake pa chiswe pamene anapha Mfilisiti uja. Choncho Yehova anachita zazikulu popambanitsa Aisraeli pa nkhondo. Inu munaona zonsezo ndipo munakondwera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwira munthu wosalakwa pofuna kupha Davide?” Sauli anamvera mawu a Yonatani ndipo analumbira kuti, “Pali Yehova, Davide sadzaphedwa.” Pambuyo pake Yonatani anayitana Davide namuwuza zonsezi. Choncho Yonatani anabwera naye Davide kwa Sauli ndipo ankamutumikira Sauliyo monga kale. Panabukanso nkhondo ina ndipo Davide anapita ndi kukamenyana ndi Afilisti. Iye anawakantha mwamphamvu kotero kuti Afilisti anathawa. Tsiku lina mzimu woyipa uja unafikanso pa Sauli. Nthawi imeneyi nʼkuti Sauli uja ali mʼnyumba mwake, mkondo uli mʼdzanja lake ndi Davide akuyimba zeze, Sauli anafuna kumubaya Davide ndi kumukhomera kukhoma, koma Davide anapewa mkondowo kotero Sauli anakabaya pa khoma. Usiku womwewo Davide anathawa. Usiku womwewo Sauli anatumiza anthu ku nyumba ya Davide kuti akamubisalire ndi kumupha mmamawa. Koma Mikala mkazi wake anamuchenjeza nati, “Ngati usiku uno supulumutsa moyo wako, mawa udzaphedwa.” Choncho Mikala anamutulutsira Davide pa zenera, ndipo anathawa ndi kupulumuka. Kenaka Mikala anatenga fano naligoneka pa bedi nayika pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwa fanolo ndipo analifunditsa nsalu. Pamene amithenga a Sauli aja anafika kuti akamugwire Davide, Mikala anati, “Davide akudwala.” Koma Sauli anatumanso anthuwo kuti akamuone Davide, nati, “Mubwere naye kuno ali pa bedi pomwepo kuti ndidzamuphe.” Koma pamene anthuwo analowa, anangoona fano pa bedipo ndi pilo wa ubweya wa mbuzi ku mutu kwake. Tsono Sauli anafunsa Mikala kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandinamiza chotere polola kuti mdani wanga athawe?” Mikala anayankha kuti, “Davide anandiwuza kuti, ‘Ukapanda kutero ndikupha.’ ” Choncho Davide anathawa napulumuka. Pambuyo pake anapita kwa Samueli ku Rama nakamuwuza zonse zimene Sauli anamuchita. Kenaka iye ndi Samueli anapita kukakhala ku Nayoti. Sauli anamva kuti, “Davide ali ku Nayoti ku Rama.” Choncho iye anatumiza anthu kuti akamugwire Davide. Koma anaona gulu la aneneri likulosera ndi Samueli akuwatsogolera. Pomwepo Mzimu wa Mulungu unawafikira ndipo nawonso anayamba kulosera. Sauli atamva zimenezi anatumizanso anthu ena, koma nawonso anayamba kulosa. Anatumanso anthu ena kachitatu, koma nawonso anayamba kulosa. Pomaliza Sauli mwini wake ananyamuka kupita ku Rama ndipo anafika ku chitsime chachikulu cha ku Seku. Ndipo anafunsa, “Samueli ndi Davide ali kuti?” Munthu wina anamuyankha kuti, “Ali ku Nayoti ku Rama.” Choncho Sauli anapita ku Nayoti ku Rama. Koma Mzimu wa Mulungu unafikanso pa iye ndipo ankalosa akuyenda mpaka anafika ku Nayoti. Nayenso anavula zovala zake nayamba kulosa pamaso pa Samueli. Kenaka anagona wamaliseche tsiku lonse ndi usiku wonse. Nʼchifukwa chake anthu amati, “Kodi Sauli alinso mmodzi wa aneneri?” Davide ndi Yonatani Tsono Davide anathawa ku Nayoti ku Rama ndi kupita kwa Yonatani ndipo anamufunsa kuti, “Kodi ine ndinachita chiyani? Kodi ndinalakwa chiyani? Kodi abambo ako ndinawalakwira chiyani kuti azifuna kundipha?” Yonatani anayankha kuti, “Sizitheka! Iwe sufa ayi! Taona abambo anga sachita chinthu chilichonse chachikulu kapena chachingʼono wosandiwuza ine. Tsopano abambo anga angandibisire bwanji zimenezi? Sichoncho ayi.” Koma Davide analumbira kuti, “Abambo ako akudziwa bwino lomwe kuti iwe umandikonda ndipo iwo amaganiza kuti, Yonatani sayenera kudziwa zimenezi mwina adzamva chisoni kwambiri. Komabe, pali Yehova ndi pali iwe, imfa sinanditalikire.” Yonatani anawuza Davide kuti, “Chilichonse chimene iwe ukufuna kuti ndichite, ndidzakuchitira.” Ndipo Davide anati, “Taona mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano, ndipo ine ndiyenera kukadya ndi mfumu. Koma undilole ndipite ndikabisale mʼmunda mpaka mkuja madzulo. Ngati abambo ako akafunsa za ine, ukawawuze kuti, ‘Davide anandiwumiriza kuti ndimulole apite msanga kwawo ku Betelehemu, chifukwa akupereka nsembe yapachaka ya banja lonse.’ Akanena kuti, ‘Wachita bwino,’ ndiye kuti zinthu zindiyendera bwino ine mtumiki wako. Koma ngati akapsa mtima, ndiye udziwe kuti iwo atsimikiza zondichita zoyipa. Koma undikomere mtima ine mtumiki wako, pakuti unapangana nane pangano pamaso pa Yehova. Ngati ndine wolakwa undiphe ndiwe, koma usandipereke kwa abambo ako.” Yonatani anati, “Sizitheka! Ndikanadziwa kuti abambo anga atsimikiza kuti akuchite choyipa, kodi sindikanakuwuza?” Davide anafunsa kuti, “Adzandiwuza ndani ngati abambo ako akuyankhe mwaukali?” Yonatani anawuza Davide kuti, “Tiyeni tikayende ku mundako.” Ndipo anapita onse awiri. Kenaka Yonatani anawuza Davide kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akhale mboni! Ine ndikadzafunsa abambo anga nthawi yonga ino mmawa kapena mkuja, ndipo ndikadzapeza kuti akukufunira zabwino, ine ndidzatuma mawu kuti udziwe. Koma ngati abambo anga atsimikiza kukuchita choyipa, Yehova andilange ine Yonatani, ndipotu kwambiri ngati sindidzakudziwitsa ndi kukulola kuti upite mu mtendere. Yehova akhale nawe monga anakhalira ndi abambo anga. Ndikakhalabe ndi moyo udzandionetse kukoma mtima monga kwa Yehova nthawi yonse ya moyo wanga, kuti ine ndisaphedwe. Ndipo usadzaleke kuchitira chifundo banja langa. Pamene Yehova adzawatha adani onse a Davide pa dziko lapansi.” “Dzina la ine Yonatani lisadzafafanizidwe nawo pamodzi. Yehova alange adani onse a Davide.” Kenaka Yonatani anamulumbiritsanso Davide kuti asaleke kumukonda, pakuti ankamukonda monga ankadzikondera yekha. Kenaka Yonatani anawuzanso Davide kuti, “Mawa ndi tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano. Zidzadziwika kuti iwe palibe chifukwa mpando wako udzakhala wopanda munthu. Mkuja adzakufunafuna. Tsono udzapite pamalo pamene unabisala poyamba paja ndipo ukadikire pa mulu wa miyala uli apowo. Ine ndidzaponya mivi itatu pambali pake, ngati ndikulasa chinthu. Ndipo ndidzatuma mnyamata ndi kuti, ‘Pita ukatole miviyo!’ Ngati ndidzanena kwa iye kuti, ‘Taona, mivi ili mbali yakuno, kayitole,’ iwe ukatuluke, pakuti ndikulumbira, pali Yehova Wamoyo, ndiye kuti zako zili bwino, palibe choopsa chilichonse. Koma ndikadzati, ‘Taona mivi ili patsogolo pako,’ iwe udzachoke chifukwa Yehova ndiye walola kuti uchokepo. Tsono zimene tapanganazi Yehova ndiye mboni pakati pa iwe ndi ine mpaka muyaya.” Choncho Davide anakabisala mʼmunda ndipo nthawi ya chikondwerero cha mwezi watsopano itakwana mfumu Sauli anadzakhala pansi kuti adye. Iye anakhala pa malo ake a nthawi zonse pafupi ndi khoma moyangʼanana ndi Yonatani, ndipo Abineri anakhala moyandikana ndi Sauli, koma pa malo a Davide panalibe munthu. Sauli sananene chilichonse tsiku limenelo pakuti ankaganiza kuti “Chilipo chimene chachitika ndi Davide. Mwina mwake ngosayenera za chipembedzo.” Koma pa tsiku lachiwiri la chikondwerero cha mwezi watsopano pamalo pa Davide panalibenso munthu. Kenaka Sauli anafunsa Yonatani kuti, “Nʼchifukwa chiyani mwana wa Yese sanabwere kudzadya, dzulo ngakhale lero?” Yonatani anayankha kuti, “Davide anandiwumiriza kuti ndimulole kuti apite ku Betelehemu. Anati, ‘Undilole ndipite, chifukwa banja lathu likupereka nsembe mu mzindamo ndipo mʼbale wanga wandiwumiriza kuti ndikakhale nawo. Ngati wandikomera mtima, chonde ndilole ndipite ndikaone abale anga.’ Nʼchifukwa chake sanabwere kudzadya ndi mfumu.” Sauli anamupsera mtima Yonatani ndipo namuwuza kuti, “Iwe mwana wobadwa mwa mkazi wamakhalidwe oyipa ndi wowukira! Kodi ukuyesa kuti ine sindikudziwa kuti umagwirizana ndi mwana wa Yese, amene akufuna kukuchititsa manyazi iwe ndi amayi ako? Mwana wa Yese akakhala ndi moyo pa dziko lapansi lino, iwe sudzakhala mfumu. Tsopano tumiza munthu akamutenge kubwera naye kwa ine, pakuti Davide ayenera kufa basi!” Yonatani anafunsa abambo ake kuti, “Nʼchifukwa chiyani mufuna kuti Davide aphedwe? Iye walakwa chiyani?” Apo Sauli anamuponyera mkondo wake kuti amuphe. Tsono Yonatani anadziwa kuti abambo ake atsimikiza mtima kuti aphe Davide. Yonatani anachoka pa tebulopo ali wopsa mtima kwambiri. Tsiku lachiwiri la chikondwererocho Yonatani sanadye chakudya. Iye anawawidwa mtima chifukwa abambo ake anatsimikiza zakupha Davide. Tsono mmawa Yonatani anapita ku munda kumene anapangana ndi Davide. Anali ndi mnyamata wake. Tsono anawuza mnyamatayo kuti, “Thamanga ukatole muvi umene nditi ndiponye.” Mnyamatayo akuthamanga Yonatani anaponya muvi patsogolo pa mnyamatayo. Mnyamatayo atafika pamene muvi wa Yonatani unagwera, Yonatani anayitananso mnyamatayo kuti, “Fulumira, pita msanga usayime.” Choncho mnyamatayo anatola muvi uja ndi kubwera nayo kwa mbuye wake. (Mnyamatayo sanadziwe chimene chimachitika koma Yonatani ndi Davide ndiwo ankadziwa). Pambuyo pake Yonatani anapereka zida zake za nkhondo kwa mnyamatayo ndipo anati, “Pita, nyamula ubwerere nazo ku mzinda.” Mnyamatayo anapita. Kenaka Davide anatuluka ku mbali ina ya mulu wa miyala uja, nadzigwetsa pansi ndi kugunditsa nkhope yake pansi katatu. Anapsompsona nayamba kulira onse awiri, koma Davide analira kwambiri. Yonatani anawuza Davide kuti, “Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’ ” Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja. Davide Apita ku Nobi Davide anapita ku Nobi kwa wansembe Ahimeleki. Ahimelekiyo ankanjenjemera pamene ankamuchingamira, ndipo anafunsa kuti, “Muli nokha chifukwa chiyani? Chifukwa chiyani mulibe wokuperekezani?” Davide anayankha Ahimeleki kuti, “Mfumu yandituma zinthu zina ndipo yandiwuza kuti, ‘Munthu aliyense asadziwe za zimene ndakutumazo.’ Kunena za anthu anga, ndawawuza kuti tikakumane pamalo pena pake. Kodi muli ndi chakudya? Patseniko malofu a buledi asanu, kapena chilichonse muli nacho.” Koma wansembeyo anamuyankha Davide kuti, “Ine ndilibe buledi wamba woti ndikupatseni. Koma pali buledi wachipembedzo yekha. Ngati anthu amene muli nawo sanagone ndi akazi awo mukhoza kudya.” Davide anayankha kuti, “Kunena zoona sitinakhudzane ndi mkazi monga timachitira nthawi zonse tikakhala pa ulendo. Anthu anga salola kudziyipitsa ndi mkazi ngakhale pa ulendo wamba. Nanji lero tili pa ulendo woterewu!” Choncho wansembe uja anamupatsa buledi wachipembedzo popeza kunalibeko buledi wina aliyense koma yekhayo amene amaperekedwa kwa Yehova. Uyu ndi amene anachotsedwa tsiku limenelo kuti ayikepo wina wotentha. Koma tsiku limenelo mmodzi wa antchito a Sauli anali pomwepo kudikirira kuti achite mwambo wa chipembedzo mʼnyumba ya Mulungu. Munthuyu dzina lake anali Doegi Mwedomu, munthu wamphamvu pakati pa abusa a Sauli. Davide anafunsa Ahimeleki kuti, “Kodi muli ndi mkondo kapena lupanga pano? Ine sindinatenge lupanga langa kapena chida china chilichonse chifukwa zimene andituma amfumu ndi zamsangamsanga.” Wansembeyo anayankha kuti, “Kuno kuli lupanga la Goliati Mfilisiti uja amene unamupha mʼchigwa cha Ela, lakulungidwa mʼnsalu paseli pa Efodi. Ngati mufuna kulitenga, tengani popeza kuno kulibe lina koma lokhalo.” Davide anati, “Palibe lina lofanana nalo. Ndipatseni lomwelo.” Davide ku Gati Tsiku lomwelo Davide ananyamuka kuthawa Sauli ndipo anapita kwa Akisi, mfumu wa ku Gati. Koma nduna za Akisi zinafunsa mfumuyo kuti, “Kodi uyu si Davide mfumu ya dzikoli? Kodi iyeyu si uja pomuvinira ankayimba kuti, “Sauli wapha 1,000, koma Davide wapha miyandamiyanda?” Mawu amenewa anamulowa kwambiri Davide mu mtima ndipo anayamba kuopa kwambiri Akisi mfumu ya ku Gati. Choncho anasintha makhalidwe ake pamaso pawo, nʼkudzisandutsa ngati wamisala. Iye ankangolembalemba pa zitseko za chipata ndi kumangotuluka dovi, nʼkumayenderera mʼndevu zake. Akisi anawuza nduna zake kuti, “Mukumuona munthu uyu kuti ndi wamisala! Nʼchifukwa chiyani mukubwera naye kwa ine? Kodi ine ndikusowa anthu amisala kuti muzibwera naye munthuyu kwa ine kuti azidzachita zamisala zake pamaso panga? Kodi munthu ameneyu nʼkulowa mʼnyumba mwanga?” Davide Apita ku Adulamu ndi ku Mizipa Davide anachoka kumeneko nathawira ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi banja lonse la abambo ake anamva izi, anapita kumene kunali Davide. Ndipo aliyense amene anali pa mavuto, kapena ndi ngongole kapenanso amene anali wosakondwa anasonkhana kwa iye, ndipo iye anakhala mtsogoleri wawo. Onse pamodzi analipo amuna 400. Kuchokera kumeneko Davide anapita ku Mizipa ku Mowabu ndipo anapempha mfumu ya Mowabu kuti, “Bwanji abambo ndi amayi anga akhale nanu mpaka ine nditadziwa chimene Mulungu adzachite nane?” Choncho iye anawasiya kwa mfumu ya Mowabu ndipo anakhala naye nthawi yonse imene Davide ankabisala ku phanga kuja. Koma mneneri Gadi anawuza Davide kuti, “Usakhale ku phanga kuno. Pita ku dziko la Yuda.” Kotero Davide anachoka ndi kupita ku nkhalango ya Hereti. Sauli Apha Ansembe a ku Nobi Tsono Sauli anamva kuti Davide ndi anthu ake apezeka. Nthawiyo nʼkuti Sauli atakhala pansi pa mtengo wa bwemba pa phiri la ku Gibeya, mkondo uli mʼdzanja lake ndi ankhondo ake atayima chomuzungulira. Tsono Sauli anafunsa ankhondo ake aja kuti, “Tamverani inu anthu a fuko la Benjamini! Kodi mwana wa Yese adzakupatsani nonsenu minda ndi minda ya mpesa? Kodi nonsenu adzakuyikani kukhala atsogoleri a magulu ankhondo? Mwinatu nʼchifukwa chake mwagwirizana zondichita chiwembu. Palibe amene anandiwuza pamene mwana wanga ankapanga pangano ndi mwana wa Yese. Palibe aliyense amene ankalabadirako za ine kapena kundiwuza kuti mwana wanga wautsa mtima wa wantchito wanga kuti andiwukire monga wachitira lero.” Koma Doegi Mwedomu anayima pafupi ndi nduna za Sauli nati, “Ine ndinaona mwana wa Yese atabwera kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi ku Nobi. Ahimelekiyo anafunsa kwa Yehova chomwe Davide ayenera kuchita. Iye anamupatsa zakudya ndiponso lupanga la Goliati Mfilisiti uja.” Pamenepo mfumu inayitanitsa wansembe Ahimeleki mwana wa Ahitubi ndi banja lonse la abambo ake, amene anali ansembe ku Nobi. Ndipo onse anabwera kwa mfumu. Sauli anati, “Tsono tamvera, mwana wa Ahitubi.” Iye anayankha kuti, “Inde mbuye wanga.” Sauli anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ndi mwana wa Yese mwandiwukira ine? Wamupatsa buledi ndi lupanga. Wafunsiranso kwa Yehova zoti andiwukire ndi kundibisalira monga wachita leromu?” Ahimeleki anayankha mfumu kuti, “Kodi ndani mwa ankhondo anu onse amene ali wokhulupirika monga Davide? Iye uja ndi mkamwini wa mfumu, kapitawo wa asilikali okutetezani ndiponso munthu amene amalemekezedwa mʼbanja lanu? Kodi tsiku limeneli linali loyamba kuti ndimufunsire kwa Yehova? Ayi sichoncho! Mfumu musandinenere kanthu kalikonse koyipa kapena banja la abambo anga, pakuti sindikudziwa kanthu kena kalikonse ka zimenezi.” Koma mfumu inati, “Iwe Ahimeleki ndi banja lonse la abambo ako mudzaphedwa ndithu.” Kenaka mfumu inalamulira alonda amene anali naye kuti, “Iphani ansembe a Yehovawa chifukwa iwo akugwirizana ndi Davide. Iwo amadziwa kuti Davide ankathawa koma sanandiwuze.” Koma antchito a mfumu aja sanasamule dzanja kuti aphe ansembe a Yehova. Kotero mfumu inalamula Doegi kuti, “Uwaphe ndiwe ansembewa.” Choncho Doegi Mwedomu anapita ndi kuwapha. Tsiku limenelo iye anapha amuna 85 amene amavala efodi wa nsalu yofewa. Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa. Koma Abiatara mwana wa Ahimeleki mwana wa Ahitubi anapulumuka ndi kuthawira kwa Davide. Abiatara anawuza Davide kuti Sauli wapha ansembe a Yehova. Ndipo Davide anati kwa Abiatara, “Tsiku lija pamene Doegi Mwedomu anali kumene kuja, ine ndimadziwa kuti salephera kukamuwuza Sauli. Ine ndi amene ndaphetsa banja lonse la abambo ako. Iwe khala ndi ine, usaope munthu amene akufuna moyo wako komanso wanga. Udzatetezeka ukakhala ndi ine.” Davide Apulumutsa Mzinda wa Keila Davide atawuzidwa kuti “Onani, Afilisti akuthira nkhondo mzinda wa Keila ndi kulanda zokolola zawo za mʼnkhokwe,” anafunsa Yehova kuti, “Kodi ndipite ndikamenyane nawo Afilistiwa?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, kamenyane nawo Afilisti ndi kupulumutsa mzinda wa Keila.” Koma anthu amene anali ndi Davide anati, “Ngati tikuchita mantha ku Yuda konkuno, nanji kupita ku Keila kukamenyana ndi ankhondo a Afilisti!” Davide anafunsanso Yehova, ndipo Yehova anamuyankha kuti, “Pita ku Keila pakuti ndapereka Afilisti mʼdzanja lako.” Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Keila kukamenyana ndi Afilisti. Anapha Afilisti ambiri ndi kutenga ziweto zawo. Choncho anapulumutsa anthu a ku Keila. (Pamene Abiatara mwana wa Ahimeleki anathawira kwa Davide anabwera ndi efodi mʼmanja mwake). Sauli Atsatira Davide Sauli atamva kuti Davide wapita ku Keila anati, “Mulungu wamupereka kwa ine, pakuti Davide wadzitsekera yekha mʼndende polowa mu mzinda umene uli ndi zipata ndi zotsekera zake.” Choncho Sauli anasonkhanitsa ankhondo ake nawatuma ku Keila kuti akamuzungulire Davide ndi anthu ake. Davide atadziwa kuti Sauli akufuna kumuchita chiwembu, anawuza Abiatara wansembe uja kuti, “Bwera nayo efodiyo.” Tsono Davide anayankhula ndi Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, ine mtumiki wanu ndamva ndithu kuti Sauli akufuna kubwera ku Keila ndi kudzawononga mzindawu chifukwa cha ine. Kodi anthu a Keila adzandipereka mʼmanja mwa Sauli? Kodi Sauli abweradi monga ndamvera ine mtumiki wanu? Inu Yehova Mulungu wa Israeli, chonde, ndiwuzeni ine mtumiki wanu.” Ndipo Yehova anati, “Sauli abweradi.” Davide anafunsanso, “Kodi anthu a ku Keila adzapereka ine ndi anthu angawa kwa Sauli?” Ndipo Yehova anayankha, “Iwo adzakuperekanidi.” Choncho Davide ndi anthu ake, omwe analipo 600, anachoka ku Keila namayenda mothawathawa. Sauli atamva kuti Davide wathawa ku Keila, sanatumizeko ankhondo ake aja. Davide ankakhala mʼmapanga mʼdziko lamapiri ku chipululu cha Zifi. Sauli ankamufufuza tsiku ndi tsiku, koma Mulungu sanapereke Davide mʼmanja mwake. Davide anaona kuti Sauli akufunafuna kuti amuphe. Nthawiyi nʼkuti Davide ali mʼchipululu cha Zifi ku Horesi. Ndipo Yonatani mwana wa Sauli anapita kwa Davide ku Horesi ndipo anamulimbitsa mtima pomuwuza kuti Yehova ali naye. Iye anamuwuza kuti, “Usaope, abambo anga sadzakupha. Iwe udzakhala mfumu ya Israeli ndipo ine ndidzakhala wachiwiri wako. Ngakhale abambo anga Sauli akudziwa zimenezi.” Awiriwa anachita pangano pamaso pa Yehova. Ndipo Yonatani anabwerera kwawo, koma Davide anakhalabe ku Horesi. Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya ndipo anamuwuza kuti, “Davide akubisala kwathu, mʼmapanga a ku Horesi, mʼphiri la Hakila, kummwera kwa Yesimoni. Tsopano inu, mubwere nthawi iliyonse imene mukufuna, ndipo ife tidzamupereka kwa mfumu.” Sauli anayankha kuti, “Yehova akudalitseni pakuti mwandichitira chifundo. Pitani mukatsimikizire. Mukaone kumene amakhala ndiponso mupeze munthu amene wamuona. Anthu amandiwuza kuti ndi wochenjera kwambiri. Kafufuzeni ndithu malo onse kumene amabisalako, ndipo mubwerenso kuno mudzandiwuze chenicheni. Pambuyo pake ine ndidzapita nanu. Ngatidi ali mʼderalo ndidzamusaka pakati pa mabanja onse a Yuda.” Kotero iwo ananyamuka ndi kupita ku Zifi, koma Sauli asananyamuke. Nthawi imeneyi Davide ndi anthu ake anali ku chipululu cha Maoni, ku Araba kummwera kwa Yesimoni. Sauli ndi anthu ake anapita kukamufufuza Davide. Koma Davide atamva izi anathawa ndi kukabisala ku thanthwe la chipululu cha Maoni. Sauli atamva kuti Davide anathawira ku Maoni anamutsatira ku chipululu komweko. Sauli amayenda mbali ina ya phirilo, ndipo Davide ndi anthu ake nawonso anali mbali ina ya phirilo. Koma Davide ndi anthu ake anafulumira kumuthawa Sauli pamene Sauliyo ndi anthu ake ali pafupi kuwagwira. Nthawi yomweyo munthu wina wamthenga anabwera kudzamuwuza Sauli kuti, “Bwerani msanga! Afilisti akuthira nkhondo dzikoli.” Choncho Sauli analeka kuthamangitsa Davide ndipo anapita kukamenyana ndi Afilisti. Nʼchifukwa chake malowa amatchedwa Mwala wa Malekano. Ndipo Davide anachoka kumeneko ndi kukakhala ku mapanga a ku Eni Gedi. Davide Amusiya Sauli Wosamupha Sauli atabwera kuchokera kumene amathamangitsa Afilisti anamva kuti, “Davide ali mʼchipululu cha Eni Gedi.” Tsono Sauli anatenga asilikali 3,000 odziwa kumenya bwino nkhondo kuchokera pakati pa Aisraeli onse ndipo anapita kukafunafuna Davide ndi anthu ake ku Matanthwe a Mbalale. Iye anafika ku makola a nkhosa amene anali mʼmbali mwa njira. Kumeneko kunali phanga, ndipo Sauli analowa mʼphangamo kuti akadzithandize. Davide ndi anthu ake ankabisala mʼkati mwenimweni mwa phangalo. Tsono anthu a Davide anamuwuza kuti, “Tsiku lija lafika limene Yehova anakuwuzani kuti, ‘Ndidzapereka mdani wanu mʼmanja mwanu, ndi kumuchita chimene chidzakukomereni.’ ” Koma Davide anapita mwakachetechete ndi kukadula msonga ya mkanjo wa Sauli. Atachita izi, Davide anatsutsika mu mtima chifukwa anadula msonga ya mkanjo wa Sauli. Tsono anawuza anthu ake kuti, “Yehova asalole kuti ndimuchite choyipa mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova. Ndisamupweteke pakuti ndi wodzozedwa wa Yehova.” Choncho Davide anabweza mitima ya anthu ake ndi mawu amenewa, ndipo sanawalole kuti aphe Sauli. Pambuyo pake Sauli anatuluka mʼphangamo ndipo anachoka. Kenaka Davide anatuluka mʼphanga muja ndipo anayitana Sauli, “Mbuye wanga!” Sauli atayangʼana mʼmbuyo, Davide anawerama ndi kugunditsa nkhope yake pansi. Anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani mumamvera mawu a anthu kuti, ‘Davide wakukonzerani chiwembu?’ Lero lino inu mwadzionera nokha kuti Yehova anakuperekani mʼmanja mwanga mʼphanga muja. Ena anandiwuza kuti ndikupheni, koma ndakusiyani. Ndinati, ‘Sindidzapha mbuye wanga pakuti ndiye wodzozedwa wa Yehova.’ Tsono abambo anga, onanitu kansalu ka mkanjo wanu kali mʼdzanja langali! Popeza kuti ndinatha kudula msonga ya mkanjo wanu koma osakuphani, pamenepo mudziwe kuti ine ndilibe maganizo woti ndikuchiteni choyipa kapena kukuwukirani. Sindinakulakwireni ngakhale kuti inu mukufuna moyo wanga kuti mundiphe. Yehova aweruze pakati pa inu ndi ine, akulangeni chifukwa cha zoyipa zimene mukundichitazi, koma dzanja langa silidzakukhudzani. Paja anthu akale anati, ‘Munthu woyipa, ntchito zakenso ndi zoyipa.’ Kotero dzanja langa silidzakukhudzani. “Kodi mfumu ya Israeli yadzalondola yani. Inu mukuthamangitsa yani? Galu wakufa kodi? Nsabwe kodi? Nʼchifukwa chake Yehova agamule, inde aweruze pakati pa inu ndi ine ndi kupeza wolakwa. Yehova anditeteze ndi kundipulumutsa mʼdzanja lanu.” Davide atatsiriza kuyankhula mawu awa, Sauli anafunsa kuti, “Kodi mawu amenewa ndi akodi mwana wanga Davide?” Sauli anayamba kulira mokweza. Anawuza Davide kuti, “Ndiwe wolungama kuposa ine. Iwe wandikomera mtima pamene ine ndakuchitira zoyipa. Iweyo lero lino wandifotokozera zabwino zimene wandichitira. Yehova anandipereka mʼdzanja lako koma iwe sunandiphe. Kodi munthu atapeza mdani wake angamulole kuti apite wosamuvulaza? Motero Yehova akuchitire iwe zabwino chifukwa cha zimene wandichitira lerozi. Ona tsono, Ine ndikudziwa kuti udzakhala mfumu ndithu ndipo ufumu wa Israeli udzakhazikika mʼmanja mwako. Tsopano undilonjeze molumbira lero mʼdzina la Yehova kuti sudzapha zidzukulu zanga ine nditamwalira kapena kufuta dzina langa pa banja la makolo anga.” Choncho Davide analumbira pamaso pa Sauli. Pambuyo pake Sauli anabwerera kwawo, koma Davide ndi anthu ake anapitanso ku phanga kuja. Davide, Nabala ndi Abigayeli Samueli anamwalira, ndipo Aisraeli onse anasonkhana kudzalira maliro ake ndipo anamuyika mʼmanda ku mudzi kwawo ku Rama. Ndipo Davide anapita ku chipululu cha Parani. Kunali munthu wina wolemera kwambiri ku Maoni amene malo ake a ntchito anali ku Karimeli. Iyeyu anali ndi mbuzi 1,000 ndi nkhosa 3,000. Dzina lake linali Nabala ndipo anali wa fuko la Kalebe. Dzina la mkazi wake linali Abigayeli. Anali mkazi wanzeru ndi wokongola, koma mwamuna wake, wa banja la Kalebe, anali wowuma mtima ndi wamwano pa zochita zake. Davide anamva akanali ku chipululu kuti Nabala akumeta nkhosa. Choncho anatuma anyamata khumi nawawuza kuti, “Pitani kwa Nabala ku Karimeli ndipo mukamulonjere mʼdzina langa. Mukamuwuze kuti, ‘Mtendere ukhale ndi inu, banja lanu pamodzi ndi zonse zimene muli nazo. “ ‘Tsono ndamva kuti muli ndi anthu ometa nkhosa. Pamene abusa anu anali nafe kuno, sitinawachite china chilichonse choyipa, ndipo sanasowe kanthu pa nthawi yonse imene anali ku Karimeli. Muwafunse antchito anu ndipo akuwuzani. Kotero akomereni mtima anyamata anga, pakuti tabwera pa nthawi yachikondwerero. Chonde apatseniko antchito anuwo ndi mwana wanu Davide chilichonse chimene mungakhale nacho.’ ” Anyamata a Davide aja atafika, anamuwuza Nabala zonse zimene Davide anayankhula. Ndipo anadikira yankho. Nabala anayankha anyamata a Davide kuti, “Kodi Davide ndi ndani? Mwana wa Yese ndi ndani? Masiku ano pali antchito ambiri amene akuthawa kwa mabwana awo. Nditengerenji buledi, madzi ndi nyama zimene ndaphera anthu anga ometa nkhosa ndi kuzipereka kwa anthu amene sindikudziwa kumene achokera?” Choncho anyamata a Davide aja anatembenuka nabwerera. Atafika anafotokozera Davide mawu onse a Nabala. Davide anawuza anthu ake kuti, “Aliyense amangirire lupanga lake!” Choncho aliyense anamangirira lupanga lake. Davidenso anamangirira lupanga lake. Anthu pafupifupi 400 ndiwo anapita ndi Davide, pamene anthu 200 anatsala ndi katundu. Tsono mmodzi mwa antchito anawuza Abigayeli mkazi wa Nabala kuti, “Davide anatumiza amithenga kuchokera ku chipululu kudzalonjera mbuye wathu, koma iye anawalalatira. Komatu anthuwa anatichitira zabwino kwambiri. Sanatizunze, ndipo nthawi yonse imene tinali nawo ku busa sitinasowe kanthu. Ankatitchinjiriza ngati mpanda usiku ndi usana nthawi yonse tinkaweta nkhosa. Tsono onani chimene mungachite, chifukwa zimenezi zingadzetse tsoka pa mbuye wathu pamodzi ndi nyumba yake. Paja mbuye athu aja ndi munthu wa khalidwe loyipa moti palibe amene angathe kuyankhula naye.” Ndipo Abigayeli sanataye nthawi. Iye anatenga malofu a buledi 200, matumba a chikopa awiri a vinyo, nkhosa zisanu zowotcheratu, makilogalamu 17 a tirigu wokazinga, makeke a mphesa zowuma 100, ndiponso makeke a nkhuyu 200, ndipo anazisenzetsa abulu. Kenaka anawuza antchito ake kuti, “Tsogolani, ine ndikutsatirani.” Koma sanawuze mwamuna wake Nabala. Mayi uja atakwera pa bulu wake ndi kufika pa tsinde la phiri, anangoona Davide ndi ankhondo ake akubwera kunali iye. Choncho anakumana nawo. Nthawiyi nʼkuti Davide atanena kuti, “Kani ndinalondera pachabe katundu wa munthu uyu mʼchipululu muja! Ndipotu palibe kanthu nʼkamodzi komwe kake kamene kanasowa. Tsono wandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino. Mulungu andilange kwambiri ngati pofika mmawa nditakhale nditasiyako ngakhale munthu mmodzi mwa onse amene ali nawo.” Abigayeli ataona Davide, anatsika pa bulu wake mofulumira ndipo anadzigwetsa pansi pamaso pa Davide. Ali chigonere choncho pa mapazi a Davide anati, “Mbuye wanga, kulakwa kukhale pa ine ndekha. Chonde lolani kuti mdzakazi wanune ndiyankhule nanu, ndipo mumve mawu a ine mdzakazi wanu. Mbuye wanga musasamale za mwamuna wanga Nabala, munthu wa khalidwe loyipa. Iyeyu ali monga dzina lake liliri. Monga dzina lake litanthauza kuti chitsiru, ndiye kuti zake zonse ndi zauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindinawaone anthu amene mbuye wanga munawatuma. Tsono mbuye wanga muli apa, ndikulumbira pali Yehova wamoyo amene wakuletsani kuti musakhetse magazi a munthu ndi kulipsira nokha, kuti adani anu amene afuna kukuchitani zoyipa adzakhale ngati Nabala. Choncho, nazi mphatso zimene mdzakazi wanu ndabwera nazo kwa mbuye wanga kuti zipatsidwe kwa anyamata amene muli nawo. Chonde khululukani zolakwa za ine mdzakazi wanu. Ndithu Yehova adzakhazikitsa banja la mbuye wanga mu ufumu, popeza mukumenya nkhondo ya Yehova. Choncho choyipa sichidzapezeka mwa inu masiku onse a moyo wanu. Ngati munthu wina akuwukirani ndi kukulondani, Yehova Mulungu wanu adzateteza moyo wa mbuye wanga monga mmene munthu asungira chuma mʼphukusi, koma moyo wa adani anu adzawutaya kutali monga momwe munthu amaponyera mwala ndi legeni. Yehova adzakuchitirani mbuye wanga zabwino zonse zimene anakulonjezani. Adzakuyikani kukhala wolamulira Aisraeli. Zikadzatero, inu mbuye wanga simudzakhala ndi chikumbumtima choti munakhetsa magazi kapena kulipsira popanda chifukwa. Koma Yehova akadzakuchitirani zabwino zonsezi musadzandiyiwale ine mdzakazi wanu.” Tsono Davide anawuza Abigayeli kuti, “Alemekezeke Yehova Mulungu wa Israeli, amene wakutuma iwe lero kuti ukumane nane. Yehova akudalitseni chifukwa cha nzeru zanu pondiletsa lero kuti ndisakhetse magazi ndi kubwezera adani anga ndi manja anga. Kunena zoona, pali Yehova Wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene wandiletsa kuti ndisakupwetekeni, mukanapanda kubwera msanga kudzakumana nane, palibe munthu aliyense wamwamuna wa Nabala akanasiyidwa wamoyo pakucha mmawa.” Ndipo Davide analandira kwa mayiyo zimene anamutengera ndipo anati, “Pitani kwanu mu mtendere. Ine ndamva mawu anu ndipo ndavomera zimene mwapempha.” Abigayeli atabwerera kwa Nabala anamupeza ali mʼnyumba akuchita mphwando ngati la mfumu. Iye anali atakondwa kwambiri popeza anali ataledzera kwambiri. Choncho mkazi wakeyo sanamuwuze kalikonse mpaka mmawa kutacha. Tsono mmawa, mowa utamuchoka Nabala, mkazi wake anamuwuza zonse. Pomwepo mtima wake unaleka kugunda ndipo unawuma gwaa ngati mwala. Patapita masiku khumi, Yehova anakantha Nabala ndipo anafa. Pamene Davide anamva kuti Nabala wamwalira, iye anati, “Alemekezeke Yehova, walipsira Nabala chipongwe chimene anandichita ndipo anandiletsa ine mtumiki wake kuti ndisachite choyipa. Yehova wabwezera pamutu pa Nabala choyipa chimene iye anachita.” Kenaka Davide anatumiza mawu kwa Abigayeli, kumupempha kuti akhale mkazi wake. Anyamata a Davide atafika ku Karimeli anawuza Abigayeli kuti, “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukhale mkazi wake.” Abigayeli anagwada nagunditsa nkhope yake pansi ndipo anati, “Ine mdzakazi wa mbuye wanga ndakonzeka kutumikira ngakhale kusambitsa mapazi a anyamata ake.” Motero Abigayeli ananyamuka mofulumira nakwera bulu wake. Tsono iye pamodzi ndi anamwali ake asanu amene ankamutumikira, anatsagana ndi amithenga a Davide aja ndipo anakakhala mkazi wake wa Davide. Davide nʼkuti atakwatiranso Ahinoamu wa ku Yezireeli ndipo onse awiri anali akazi ake. Koma Sauli anali atakwatitsa Mikala, mkazi wa Davide kwa Paliti mwana wa Laisi wa ku Galimu. Davide Apewa Kupha Sauli Kachiwiri Anthu a ku Zifi anapita kwa Sauli ku Gibeya nati, “Davide akubisala ku phiri la Hakila, limene limayangʼanana ndi Yesimoni.” Choncho Sauli ananyamuka pamodzi ndi ankhondo ake 3,000 napita ku chipululu cha Zifi kukafunafuna Davide ku chipululuko. Sauli anamanga msasa wake mʼmbali mwa njira yopita ku phiri la Hakila moyangʼanana ndi Yesimoni. Koma Davide anali mʼchipululumo. Davide ataona kuti Sauli amamulondola mpaka kumeneko, iye anatumiza anthu okazonda ndipo anapeza kuti Sauli wafikadi ndithu. Tsono Davide ananyamuka napita kumalo kumene Sauli anamanga misasa. Iye anaona pamene Sauli ndi Abineri mwana wa Neri mkulu wa ankhondo anagona. Sauli anagona mʼkati mwa tenti ndipo asilikali anagona momuzungulira. Ndipo Davide anafunsa Ahimeleki Mhiti ndi Abisai mwana wa Zeruya, mʼbale wa Yowabu kuti, “Ndani adzapita nane ku msasa kwa Sauli?” Abisai anayankha kuti, “Ine ndidzapita nanu.” Choncho Davide ndi Abisai anapita ku misasa ya ankhondowo usiku. Atafika anangopeza Sauli ali gone mu msasa wake mkondo wake atawuzika pansi pafupi ndi mutu wake, Abineri ndi ankhondo onse anali atagona momuzungulira. Abisai anawuza Davide kuti, “Lero Mulungu wapereka mdani wanu mʼmanja mwanu. Tsopano ndiloleni ndimukhomere pansi ndi mkondo wangawu kamodzinʼkamodzi. Sindimulasa kawiri.” Koma Davide anamuyankha Abisai kuti, “Usamuphe! Ndani adzapha wodzozedwa wa Yehova ndi kupezeka wosalakwa? Davide anati, Pali Yehova wamoyo, Yehova mwini ndiye adzamukanthe, mwina tsiku lake lomwalira lidzafika, kapena adzapita ku nkhondo nakaphedwa komweko. Koma Yehova andiletse kuti ndisapweteke wodzozedwa wa Yehova. Tsopano tingotenga mkondo umene uli ku mutu kwakewo ndi botolo la madzilo ndipo tizipita.” Motero Davide anatenga mkondo ndi botolo lamadzi zimene zinali ku mutu kwa Sauli ndipo anachoka. Palibe amene anaona zimenezi kapena kudziwa, ndipo palibenso amene anadzuka. Onse anali mʼtulo, chifukwa Yehova anawagonetsa tulo tofa nato. Pambuyo pake Davide anadutsa nakakwerera mbali ina ya phiri, ndi kuyimirira pamwamba pa phiri patali. Pakati pawo panali mpata waukulu. Davide anayitana gulu lankhondo ndi Abineri mwana wa Neri nawafunsa kuti, “Kodi sundiyankha ine Abineri?” Abineri anayankha kuti, “Ndiwe yani amene ukuyitana mfumu?” Davide anamufunsa Abineri kuti, “Kodi sindiwe mwamuna? Ndipo wofanana nawe ndani mu Israeli? Nʼchifukwa chiyani sunateteze mbuye wako mfumu? Munthu wina anabwera kumeneko. Chimene wachita iwe si chabwino. Pali Yehova wamoyo iwe ndi asilikali ako muyenera kufa chifukwa simunateteze mbuye wanu, wodzozedwa wa Yehova. Tayangʼanayangʼana. Uli kuti mkondo wa mfumu ndi botolo lamadzi zimene zinali kumutu kwa mfumu?” Sauli anazindikira mawu a Davide ndipo anafunsa kuti, “Kodi amenewa ndi mawu ako Davide mwana wanga?” Davide anayankha, “Inde ndi anga, mbuye wanga mfumu. Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukundilonda ine mtumiki wanu? Kodi ine ndachita chiyani ndipo ndapezeka ndi cholakwa chotani? Tsopano mbuye wanga mfumu tamverani mawu a mtumiki wanu. Ngati ndi Yehova wautsa mtima wanu kuti mundiwukire, ndiye alandire chipepeso. Koma ngati ndi anthu amene achita zimene, ndiye Yehova awatemberere popeza andipirikitsa lero kundichotsa mʼdziko la Yehova, namati, ‘Pita kapembedze milungu ina.’ Tsopano musalole kuti magazi anga akhetsedwe kutali ndi Yehova pakuti mfumu ya Israeli yatuluka kudzafunafuna ine nsabwe, monga mmene munthu asakira nkhwali ku mapiri.” Ndipo Sauli anati, “Ine ndachimwa. Bwerera mwana wanga Davide. Sindidzakuchitanso choyipa popeza lero wauwona moyo wanga ngati wamtengowapatali. Taona, ndachita zauchitsiru ndipo ndachimwa kwambiri.” Davide anayankha kuti, “Nawu mkondo wanu, mfumu. Tumani mmodzi wa anyamata anu abwere adzatenge. Yehova amadalitsa munthu aliyense wolungama ndi wokhulupirika. Yehova anakuperekani lero mʼmanja mwanga, koma ine sindinakhudze wodzozedwa wa Yehova. Monga momwe ine lero ndachitira kuwuyesa moyo wanu ngati wamtengowapatali, momwemonso Yehova awuyese moyo wanga wamtengowapatali ndipo andipulumutse mʼmavuto anga onse.” Ndipo Sauli anawuza Davide kuti, “Yehova akudalitse iwe Davide mwana wanga. Udzachita zinthu zazikulu ndipo udzapambana.” Choncho Davide anayenda njira yake ndipo Sauli anabwerera kwawo. Davide Pakati pa Afilisti Davide anaganiza mu mtima mwake nati, “Tsiku lina ine ndidzaphedwa ndi Sauli. Palibe chabwino ndingachite, koma kuthawira ku dziko la Afilisti. Kotero Sauli adzasiya kundifunafuna mʼdziko lonse la Israeli, ndipo ndidzapulumuka.” Choncho Davide ndi anthu 600 amene anali nawo anachoka napita kwa Akisi mwana wa Maoki mfumu ya ku Gati. Davide anakhala ndi Akisi ku Gati pamodzi ndi ankhondo ake, aliyense ndi banja lake. Davide ali ndi akazi ake awiri, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wamasiye wa Nabala. Sauli anamva kuti Davide wathawira ku Gati, ndipo sanamufunefunenso. Kenaka Davide anawuza Akisi kuti, “Ngati ndapeza kuyanja pamaso panu mundipatse malo dera limodzi la dziko lanu kuti ndizikhala kumeneko. Mtumiki wanu adzakhala mu mzinda waufumu chifukwa chiyani?” Choncho tsiku limenelo Akisi anamupatsa Zikilagi ndipo mzindawo wakhala wa mafumu a Yuda mpaka lero. Davide anakhala mʼdziko la Afilisti kwa chaka chimodzi ndi miyezi inayi. Tsono Davide ndi anthu ake ankapita kukathira nkhondo Agesuri, Agirizi ndi Aamaleki. (Mitundu ya anthu imeneyi kuyambira kale inkakhala mʼdziko la pakati pa Suri ndi Igupto). Davide ankati akathira nkhondo dera lina, sankasiya munthu wamoyo, mwamuna kapena mkazi, koma ankatenga nkhosa, ngʼombe, abulu, ngamira ndi zovala, pambuyo pake nʼkubwerera kwa Akisi. Akisi akafunsa kuti, “Kodi lero unapita kukathira nkhondo kuti?” Davide ankayankha kuti, “Ndinapita kukathira nkhondo kummwera kwa Yuda,” mwinanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Ayerahimeeli” kapenanso ankanena kuti, “Ndinapita ku dziko la Akeni.” Davide sankasiya mwamuna kapena mkazi wamoyo kuti akafotokozere anthu a ku Gati zochitikazo kuopa kuti opulumukawo akhoza kudzanena kuti “Davide watichita zakutizakuti.” Tsono izi ndi zimene Davide ankachita pamene ankakhala mʼdziko la Afilisti. Akisi ankamukhulupirira Davide ndipo ankati mu mtima mwake, “Davide wadzisandutsa munthu woyipa kwambiri pakati pa anthu ake omwe, Aisraeli. Tsono adzakhala mtumiki wanga mpaka kalekale.” Sauli ndi Mfiti ya ku Endori Mʼmasiku amenewo Afilisti anasonkhanitsa ankhondo awo kuti akamenyane ndi Aisraeli. Akisi anawuza Davide kuti, “Udziwe kuti iwe pamodzi ndi anthu ako mudzapita nane ku nkhondo.” Davide anayankha kuti, “Tsono inu mudzaona zimene mtumiki wanune ndingachite.” Akisi anayankha kuti, “Chabwino ine ndidzakuyika iwe kukhala mlonda wanga moyo wako wonse.” Nthawi imeneyi nʼkuti Samueli atamwalira, ndipo Aisraeli onse anamulira namuyika mʼmanda ku mzinda wake wa Rama. Sauli anali atachotsa mʼdzikomo anthu owombeza mawula ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Tsono Afilisti anasonkhana nabwera kudzamanga misasa yawo ku Sunemu. Nayenso Sauli anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kumanga misasa yawo ku Gilibowa. Sauli ataona gulu lankhondo la Afilisti anaopa ndipo ananjenjemera kwambiri. Choncho Sauli anafunsa nzeru kwa Yehova koma Yehova sanamuyankhe ngakhale kudzera mʼmaloto, kapena mwa Urimu ngakhalenso kudzera mwa aneneri. Kenaka Sauli anawuza nduna zake kuti, “Mundipezere mkazi amene amawombeza mawula kuti ndipite ndikafunse kwa iye.” Nduna zakezo zinamuyankha kuti, “Alipo mkazi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa ku Endori.” Kotero Sauli anadzizimbayitsa navala zovala zachilendo. Tsono iye pamodzi ndi anthu awiri anapita nakafika kwa mkazi uja usiku, ndipo anamupempha kuti, “Chonde ndifunsireni nzeru kwa mizimu ya anthu akufa. Koma makamaka munditulutsire mzimu wa amene ndimutchule.” Koma mkaziyo anayankha kuti, “Ndithu inu mukudziwa chimene Sauli anachita. Paja iye anachotsa mʼdziko muno anthu onse owombeza ndi woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Chifukwa chiyani mukutchera moyo wanga msampha kuti ndiphedwe?” Koma Sauli analonjeza mkaziyo molumbira nati, “Pali Yehova wamoyo, iweyo sudzalangidwa chifukwa cha zimenezi.” Kenaka mkaziyo anafunsa, “Ndikuyitanireni yani?” Iye anati, “Undiyitanire Samueli.” Pamene mkaziyo anaona Samueli anakuwa kwambiri, nawuza Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani inu mwandipusitsa? Inu ndinu Sauli!” Mfumuyo inamuwuza kuti, “Usaope. Kodi ukuona chiyani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Ndikuona mzimu ukutuluka pansi.” Sauli anafunsa, “Kodi mzimuwo ukuoneka motani?” Mkaziyo anayankha kuti, “Amene akutuluka ndi munthu wokalamba ndipo wavala mkanjo.” Apo Sauli anadziwa kuti anali Samueli ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi. Samueli anafunsa Sauli kuti, “Nʼchifukwa chiyani wandivutitsa pondiyitana kuti ndibwere kuno?” Sauli anayankha kuti, “Ine ndavutika kwambiri mʼmaloto. Afilisti akumenyana nane, ndipo Mulungu wandifulatira. Iye sakundiyankhulanso, ngakhale kudzera mwa aneneri kapena maloto. Choncho ndakuyitanani kuti mundiwuze zoti ndichite.” Samueli anati, “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa ine, pakuti tsopano Yehova wakufulatira ndipo wasanduka mdani wako? Yehova wakuchita zimene ananeneratu kudzera mwa ine. Yehova wachotsa ufumu mʼmanja mwako ndipo waupereka kwa mnansi wako, kwa Davide. Yehova wachita zimenezi lero chifukwa sunamvere mawu ake ndipo sunawawonongeretu Aamaleki. Yehova adzapereka ndithu iweyo pamodzi ndi Aisraeli kwa Afilisti. Ndipo mmawa iweyo ndi ana ako mudzakhala ndi ine kuno. Ndithu Yehova adzapereka gulu lankhondo la Aisraeli kwa Afilisti.” Nthawi yomweyo Sauli anagwa pansi atadzazidwa ndi mantha chifukwa cha mawu a Samueli. Analibenso mphamvu, pakuti sanadye tsiku lonse. Mkazi uja tsono anasendera kufupi ndi Sauli, ndipo ataona kuti Sauli akuchita mantha, anamuwuza kuti, “Taonani, mdzakazi wanune ndakumverani. Ndayika moyo wanga pa chiswe ndipo ndamvera zimene munandiwuza. Tsono inunso mumvere mawu a mdzakazi wanune. Mundilole kuti ndikupatseni ka buledi pangʼono kuti mukhale ndi mphamvu zoyendera pa ulendo wanu.” Iye anakana ndipo anati, “Ayi, ine sindidya.” Koma nduna zake pamodzi ndi mkaziyo anamuwumiriza, ndipo anawamvera. Choncho anadzuka pansi nakhala pa bedi. Mkaziyo anali ndi mwana wangʼombe wonenepa ndipo anamupha mwachangu. Anatenga ufa nawukanyanga ndipo anaphika buledi wopanda yisiti. Tsono anapereka bulediyo kwa Sauli ndi nduna zake ndipo anadya. Pambuyo pake ananyamuka kupita kwawo usiku womwewo. Afilisti Akana Davide Afilisti anasonkhanitsa asilikali awo onse ku Afeki, ndipo Israeli anamanga misasa yawo pa chitsime cha Yezireeli. Pamene atsogoleri a Afilisti ankatsogolera magulu awo ankhondo a miyandamiyanda, Davide ndi ankhondo ake ankayenda pambuyo pamodzi ndi Akisi. Tsono atsogoleri a Afilisti aja anafunsa kuti, “Kodi Ahebri awa akufuna chiyani?” Akisi anayankha kuti, “Uyu ndi Davide, mtumiki wa Sauli mfumu ya Israeli. Iye wakhala ndi ine kwa masiku ndithu, kapena titi zaka ndipo kuyambira tsiku limene anachoka kwa Sauli mpaka lero, ine sindinapeze cholakwa mwa iye.” Koma atsogoleri a ankhondo a Afilisti anamukwiyira Akisi kwambiri ndipo anati, “Mubweze munthuyu kuti abwerere ku malo amene unamupatsa. Iye asapite nafe ku nkhondo kuopa kuti angadzasanduke mdani wathu. Kodi iyeyu adzadziyanjanitsa bwanji ndi mbuye wake? Iyeyutu adzadziyanjanitsa ndi mbuye wake pakupha anthu ali panowa? Paja ameneyu ndi Davide yemwe ankamuvinira namuyimbira kuti, “ ‘Sauli wapha anthu 1,000 koma Davide wapha miyandamiyanda?’ ” Kotero Akisi anayitana Davide ndipo anamuwuza kuti, “Pali Yehova wamoyo, iwe wakhala wodalirika ndipo chikanakhala chinthu chabwino kuti uzimenya nkhondo pamodzi nane popeza chibwerere iwe kuno ine sindinapeze cholakwa chilichonse ndi iwe. Koma atsogoleri enawa ndiwo sakukufuna. Tsono bwerera. Upite mu mtendere kuopa kuti ungachite kanthu kena koyipira atsogoleri a Afilistiwa.” Davide anafunsa Akisi kuti, “Kodi ndachita chiyani? Kodi mwapeza cholakwa chotani mwa ine mtumiki wanu chiyambire kukutumikirani mpaka lero? Tsono chifukwa chiyani sindingapite kukamenya nkhondo ndi adani a mbuye wanga mfumu?” Akisi anayankha kuti, “Ine ndikudziwa kuti ndiwe wangwiro ngati mngelo wa Mulungu. Komabe atsogoleri a ankhondo a Afilisti akuti, ‘Davide asapite nafe ku nkhondo.’ Tsono udzuke mmamawa, pamodzi ndi ankhondo ako amene unabwera nawo, ndipo unyamuke kukangocha.” Choncho Davide ndi anthu ake anadzuka mmamawa kubwerera ku dziko la Afilisti. Koma Afilistiwo anapita ku Yezireeli. Davide Amenyana ndi Aamaleki Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto. Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo. Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo. Kotero Davide ndi anthu ake analira mofuwula mpaka analibenso mphamvu zolirira. Akazi awiri a Davide, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli anatengedwanso. Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake. Kenaka Davide anawuza wansembe Abiatara, mwana wa Ahimeleki kuti, “Ndipatse efodi ija.” Abiatara anabwera nayo efodiyo. Tsono Davide anapempha nzeru kwa Yehova nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondoli? Kodi ndidzawapambana?” Yehova anayankha kuti, “Litsatire, iwe udzawapambana ndithu ndipo udzapulumutsa anthu ako.” Davide pamodzi ndi anthu ake 600 aja ananyamuka nafika ku mtsinje wa Besori. Kumeneko anasiyako anthu ena. Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja. Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye. Anamupatsanso chidutswa cha keke yankhuyu ndi makeke awiri a mphesa zowumika kuti adye. Atadya anapezanso mphamvu popeza anakhala masiku atatu wosadya kapena kumwa kanthu kalikonse. Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?” Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo. Ife tinathira nkhondo dera la kummwera kwa mayiko a Akereti, dera la Yuda, ndi dera la kummwera kwa mayiko a Kalebe. Mzinda wa Zikilagi tinawutentha ndi moto.” Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?” Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.” Mwigupto uja anaperekeza Davide. Tsono Aamaleki anali atamwazikana ponseponse. Iwo ankadya, kumwa ndi kuvina chifukwa cha zofunkha zambiri zimene anatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Ayuda. Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa. Choncho Davide analanditsa zinthu zonse zimene Aamaleki aja anatenga. Anapulumutsanso akazi ake awiri aja. Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja. Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.” Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera. Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.” Koma Davide anawayankha kuti, “Ayi, abale anga, musachite zimenezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watisunga ndi kupereka mʼmanja mwathu gulu la ankhondo limene linabwera kudzalimbana nafe. Ndani angakumvereni zimene mukunenazi? Gawo la munthu amene anapita kukamenya nkhondo likhale lofanana ndi la munthu amene anatsala pano kuyangʼanira katundu wathu. Pasakhale kusiyana kulikonse.” Choncho Davide anakhazikitsa ngati lamulo mʼchitidwe woterewu pakati pa Aisraeli kuyambira tsiku limenelo mpaka lero. Davide atafika ku Zikilagi, anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa akuluakulu a Yuda, amene anali abwenzi ake. Anati, “Nayi mphatso yanu yochokera pa zofunkha za adani a Yehova.” Iye anatumiza mphatsozo kwa anthu a ku Beteli, Ramoti-Negavi, Yatiri, Aroeri, Sifimoti, Esitemowa Rakala, mizinda ya fuko la Ayerahimeeli, mizinda ya fuko la Akeni, a ku Horima, Borasani, Ataki, Hebroni pamodzi ndi onse a kumalo kumene Davide ndi anthu ake anakhala akuyendayendako. Imfa ya Sauli ndi Ana Ake Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza kwambiri. Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere kudzandizunza ine.” Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa naye limodzi. Motero Sauli ndi ana ake atatu, wonyamula zida zake pamodzi ndi anthu ake onse anafera limodzi pa tsikulo. Pamene Aisraeli amene anali tsidya lina la chigwa ndi amene anali tsidya la chigwa cha Yorodani anaona kuti gulu la ankhondo la Aisraeli lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo. Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa anapeza Sauli ndi ana ake atatu atafa pa phiri la Gilibowa. Iwo anadula mutu wake ndi kumuvula zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba yopembedzera Asitoreti, ndipo thupi lake analikhomera pa khoma la mzinda wa Beti-Sani. Pamene anthu a ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, anthu awo onse olimba mtima anayenda usiku wonse kupita ku Beti-Sani. Anakachotsa mtembo wa Sauli ndi mitembo ya ana ake pa khoma la mzinda wa Beti-Sani, ndipo anabwera nayo ku Yabesi kumene anayitentha ndi moto. Pambuyo pake anatenga mafupa awo ndi kuwakwirira pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri.