- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016
1 MAFUMU
1 Mafumu
1 Mafumu
1 Maf
1 Mafumu
Adoniya Adziyika Kukhala Mfumu
Mfumu Davide atakalamba sankamva kufunda ngakhale akamufunditsa mabulangeti. Choncho nduna zake zinamuwuza kuti, “Tiloleni tifune namwali woti azikhala nanu ndi kumakusamalirani. Namwaliyo azigona pafupi nanu kuti mbuye wathu mfumu muzimva kufundira.”
Kotero anafunafuna mʼdziko lonse la Israeli mtsikana wokongola ndipo anapeza Abisagi wa ku Sunemu, nabwera naye kwa mfumu. Mtsikanayo anali wokongola kwambiri ndipo ankasamalira mfumu ndi kumayitumikira, koma mfumuyo sinakhale naye malo amodzi.
Nthawi imeneyi Adoniya, mwana wa Hagiti, anayamba kudzitukumula ndipo anati, “Ndidzakhala mfumu ndine.” Choncho anadzikonzera galeta ndi akavalo, pamodzi ndi anthu 50 woti azithamanga patsogolo pake. (Abambo ake sanalowererepo nʼkamodzi komwe ndipo sanafunsepo kuti, “Nʼchifukwa chiyani ukuchita zimenezi?” Adoniyayo anali wokongola kwambiri ndipo anali wopondana ndi Abisalomu).
Adoniya anagwirizana ndi Yowabu mwana wa Zeruya ndiponso Abiatara wansembe, ndipo iwowa anamuthandiza. Koma Zadoki wansembe, Benaya mwana wa Yehoyada, mneneri Natani, Simei ndi Rei ndiponso asilikali amphamvu a Davide sanamutsate Adoniya uja.
Kenaka Adoniya anapereka nsembe za nkhosa ndi ngʼombe ndiponso ana angʼombe onenepa ku Mwala wa Zohereti kufupi ndi Eni Rogeli. Iye anayitana abale ake onse, ana aamuna a mfumu ndiponso akuluakulu onse a ku Yuda, koma sanayitane mneneri Natani kapena Benaya kapenanso asilikali amphamvu a Davide ngakhalenso mʼbale wake Solomoni.
Pamenepo Natani anafunsa Batiseba, amayi ake a Solomoni, kuti, “Kodi simunamve kuti Adoniya, mwana wa Hagiti, walowa ufumu popanda Davide mbuye wathu kudziwa? Tsopano ine ndikulangizeni inu mmene mungapulumutsire moyo wanu ndi moyo wa mwana wanu Solomoni. Pitani msanga kwa Mfumu Davide ndipo mukanene kuti, ‘Mbuye wanga mfumu, kodi simunalumbire kwa ine mdzakazi wanu kuti, ‘Ndithu mwana wako Solomoni ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwanga, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu?’ Nanga nʼchifukwa chiyani Adoniya walowa ufumu?’ Pamene inu muzikayankhula ndi mfumu, ine ndidzalowa ndi kuchitira umboni mawu anuwo.”
Choncho Batiseba anapita nakalowa ku chipinda kukaonana ndi mfumu imene inali itakalamba kwambiri, kumene Abisagi wa ku Sunemu uja ankayisamalira. Batiseba anagwada nalambira mfumu.
Mfumu inamufunsa kuti, “Kodi nʼchiyani chimene ukufuna?”
Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga, inu mwini munalumbira kwa ine mdzakazi wanu mʼdzina la Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Solomoni mwana wako ndiye adzakhale mfumu mʼmalo mwa ine, ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.’ Koma tsopano Adoniya ndiye walowa ufumu, ndipo inu mbuye wanga mfumu, simukuzidziwa zimenezi. Ndipo wapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndi nkhosa ndi mbuzi ndipo wayitana ana anu onse, wansembe Abiatara ndiponso Yowabu mkulu wa ankhondo, koma sanayitane kapolo wanu Solomoni. Mbuye wanga mfumu, maso a Aisraeli onse ali pa inu, kuti adziwe kuchokera kwa inu amene adzakhala pa mpando waufumu wa mbuye wanga mʼmalo mwanu. Mukapanda kutero, mbuye wanga, mukadzangotisiya nʼkulondola kumene kunapita makolo anu, ine pamodzi ndi mwana wangayu Solomoni adzatiyesa owukira.”
Pamene Batiseba amayankhula ndi mfumu, mneneri Natani analowa. Ndipo anthu anawuza mfumu kuti, “Kwabwera mneneri Natani.” Kotero iye anafika pamaso pa mfumu ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi.
Natani anafunsa kuti, “Mbuye wanga mfumu, kodi mwalengeza kuti Adoniya adzakhala mfumu mʼmalo mwanu, ndi kuti adzakhala pa mpando wanu waufumu? Lero lomwe lino wakapereka nsembe ngʼombe zambiri, ana angʼombe onenepa ndiponso nkhosa ndi mbuzi. Iye wayitana ana anu onse, atsogoleri a nkhondo, ndiponso wansembe Abiatara. Panopa onsewa akudya ndi kumwa naye ndipo akunena kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Adoniya!’ Koma ine kapolo wanu, wansembe Zadoki ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndiponso kapolo wanu Solomoni sanatiyitane. Kodi zimenezi mbuye wanga mfumu mwazichita ndinu, osawawuza atumiki anu kuti adziwe amene adzakhale pa mpando waufumu mʼmalo mwanu?”
Davide Alonga Ufumu Solomoni
Pamenepo mfumu Davide anati, “Muyitaneni Batiseba.” Kotero Batiseba analowa ndipo anayimirira pamaso pa mfumu.
Tsono mfumu inalumbira kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene anandipulumutsa ine ku mavuto onse, ndithu ine lero ndichita zonse zimene ndinalumbira kwa Yehova Mulungu wa Israeli kuti, mwana wako Solomoni adzakhala mfumu mʼmalo mwanga ndipo adzakhala pa mpando wanga waufumu.”
Pamenepo Batiseba anawerama, nagunditsa mutu wake pansi nalambira mfumu, ndipo anati, “Mbuye wanga Mfumu Davide mukhale ndi moyo wautali!”
Mfumu Davide anati, “Ndiyitanireni wansembe Zadoki, mneneri Natani ndi Benaya mwana wa Yehoyada.” Atafika pamaso pa mfumu, mfumuyo inati kwa iwo, “Tengani atumiki anga ndipo mukweze mwana wanga Solomoni pa bulu wanga ndipo mupite naye ku Gihoni. Mukalize lipenga ndi kufuwula kuti, ‘Akhale ndi moyo wautali mfumu Solomoni!’ Kumeneko Zadoki wansembe ndi mneneri Natani akamudzoze kuti akhale mfumu ya Israeli. Kenaka mukalize lipenga ndi kumanena kuti ‘Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni.’ Ndipo pobwera muzikamutsata pambuyo. Iyeyo akabwere kuno ndi kudzakhala pa mpando wanga waufumu ndi kudzalamulira mʼmalo mwanga. Ndamusankha kukhala wolamulira Israeli ndi Yuda.”
Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti, “Ameni! Yehova Mulungu wa mbuye wanga mfumu akhazikitse kuti zichitike motero. Monga momwe Yehova wakhalira ndi inu mbuye wanga mfumu, momwemonso akhale ndi Solomoni ndi kukhazikitsa ufumu wake kuti ukhale waukulu kuposa ufumu wa mbuye wanga Mfumu Davide!”
Kotero Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndiponso Apeleti, anthu oteteza mfumu, anapita kukamukweza Solomoni pa bulu wa Mfumu Davide ndi kupita naye ku Gihoni. Wansembe Zadoki anatenga nyanga ya mafuta yochokera ku malo opatulika ndi kumudzoza Solomoni. Kenaka analiza lipenga ndipo anthu onse anafuwula kuti, “Akhale ndi moyo wautali Mfumu Solomoni!” Ndipo anthu onsewo anapita namutsatira pambuyo akuyimba zitoliro ndi kukondwerera kwambiri, kotero nthaka inagwedezeka chifukwa cha phokoso lawo.
Adoniya pamodzi ndi anthu onse oyitanidwa amene anali naye anamva zimenezi pamene ankamaliza madyerero awo. Atamva kulira kwa malipenga, Yowabu anafunsa kuti, “Kodi phokoso lonselo mu mzindamo likutanthauza chiyani?”
Iye akuyankhula, Yonatani mwana wa wansembe Abiatara anafika. Adoniya anati, “Lowa. Munthu wabwino ngati iwe ayenera kubweretsa nkhani yabwino.”
Yonatani anayankha Adoniya kuti, “Ayi ndithu, zinthu sizili bwino! Mbuye wathu Mfumu Davide walonga Solomoni ufumu. Mfumu yatuma Zadoki wansembe, mneneri Natani, Benaya mwana wa Yehoyada, Akereti ndi Apeleti ku Gihoni ndipo iwo amukweza pa bulu wa mfumu, ndipo Zadoki wansembe ndi mneneri Natani adzoza Solomoni ku Gihoni kuti akhale mfumu. Ndipo kuchokera kumeneko akhala akululutira, kotero kuti mu mzinda monse muli phokoso lokhalokha. Ndiyetu phokoso limene mukulimvalo. Ndipo Solomoni wakhala kale pa mpando wake waufumu. Kuwonjezera pamenepo, nduna za mfumu zabwera kale kudzayamika mbuye wathu Mfumu Davide, pomanena kuti, ‘Mulungu wanu atchukitse dzina la Solomoni kuposa dzina lanu ndipo ufumu wake ukule kupambana ufumu wanu!’ Ndipo mfumu inawerama niyamba kupembedza pa bedi lake, inati, ‘Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wasankha wolowa mʼmalo mwanga ine ndikanali ndi moyo lero lino.’ ”
Anthu onse amene Adoniya anawayitana ananjenjemera ndi mantha, ndipo anayimirira, kenaka anamwazikana. Koma Adoniya, poopa Solomoni, anapita ku Nyumba ya Mulungu nakagwira msonga za guwa lansembe. Tsono Solomoni anawuzidwa kuti, “Adoniya akukuopani inu Mfumu Solomoni ndipo wagwira msonga za guwa lansembe. Iye akuti, ‘Mfumu Solomoni alumbire kuti sadzapha kapolo wake ndi lupanga.’ ”
Solomoni anayankha kuti, “Ngati iyeyo aonetse kuti ndi munthu wakhalidwe labwino, ngakhale tsitsi la mʼmutu mwake silidzathothoka ndi kugwera pansi, koma akapezeka kuti ali ndi khalidwe loyipa, adzafa ndithu.” Pamenepo Mfumu Solomoni inatuma anthu ndipo anakamutenga paguwa paja. Adoniya anabwera ndi kudzalambira Mfumu Solomoni, ndipo Solomoni anati, “Pita ku nyumba yako.”
Davide Alangiza Solomoni
Davide ali pafupi kumwalira, analangiza mwana wake Solomoni kuti:
“Ndatsala pangʼono kupita kumene munthu wina aliyense amayenera kupitako. Tsono khala wamphamvu, uvale zilimbe, ndipo uzichita zimene Yehova Mulungu wako amafuna, uziyenda mʼnjira zake, uzisunga malangizo ndi malamulo ake monga momwe zinalembedwera mʼMalamulo a Mose, kuti zonse zimene udzachite zidzakuyendere bwino kulikonse kumene udzapite. Ndipo Yehova akwaniritse zimene anandilonjeza kuti, ‘Ngati zidzukulu zako zidzakhala mosamala, niziyenda mokhulupirika pamaso panga ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse, sudzasowa munthu wokhala pa mpando waufumu wa Israeli.’
“Tsono iwe ukudziwanso zoyipa zimene Yowabu mwana wa Zeruya anandichitira pakupha atsogoleri awiri a ankhondo a Israeli, Abineri mwana wa Neri ndi Amasa mwana wa Yeteri. Iye anawapha ndi kukhetsa magazi nthawi ya mtendere ngati nthawi ya nkhondo, ndipo anapaka magazi amenewo pa lamba wa mʼchiwuno mwake ndi pa nsapato za ku mapazi ake. Iwe uchite kwa iye molingana ndi nzeru zako, koma usalole kuti afe ndi ukalamba ndi kupita ku manda mwamtendere.
“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.
“Ndipo kumbukira kuti uli ndi Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wochokera ku Bahurimu, amene ananditemberera koopsa tsiku limene ndimapita ku Mahanaimu. Atabwera kudzakumana nane ku Yorodani, ine ndinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Sindidzakupha iwe ndi lupanga.’ Koma tsopano usamuyese ngati munthu wosalakwa. Iwe ndiwe munthu wanzeru. Udzadziwa choti uchite naye. Ngakhale ndi wokalamba, aphedwe ndithu.”
Tsono Davide anamwalira ndipo anayikidwa mʼmanda mu Mzinda wa Davide. Iyeyo nʼkuti atalamulira Israeli kwa zaka makumi anayi. Ku Hebroni analamulira zaka zisanu ndi ziwiri ndipo ku Yerusalemu analamulira zaka 33. Choncho Solomoni anakhala pa mpando waufumu wa abambo ake Davide, ndipo ufumu wake unakhazikika kwambiri.
Kukhazikika kwa Ufumu wa Solomoni
Tsono Adoniya, mwana wa Hagiti, anapita kwa Batiseba, amayi ake a Solomoni. Batiseba anamufunsa kuti, “Kodi wabwera mwamtendere?”
Iye anayakha kuti, “Eya, ndi zamtendere.” Ndipo iye anawonjezera kunena kuti, “Ndili ndi mawu oti ndiyankhule nanu.”
Batiseba anayankha kuti, “Yankhula.”
Tsono Adoniya anati, “Monga inu mukudziwa, ufumu unali wanga. Aisraeli onse ankayembekezera kuti ine ndidzakhala mfumu yawo. Koma zinthu zinasintha ndipo ufumu wapita kwa mʼbale wanga; pakuti wapatsa iye ufumuwu ndi Yehova. Tsono ndili ndi pempho limodzi kwa inu. Musandikanize ayi.”
Batiseba anati, “Nena.”
Adoniya anapitiriza kunena kuti, “Chonde, inu mupemphe mfumu Solomoni kuti andipatse Abisagi wa ku Sunemu kuti akhale mkazi wanga pakuti mukapempha inu sadzakukanizani.”
Batiseba anayankha kuti, “Chabwino. Ndidzakuyankhulira kwa mfumu.”
Batiseba atapita kwa Mfumu Solomoni kukayankhula naye mʼmalo mwa Adoniya, mfumu inanyamuka kukumana naye, ndipo inaweramira amayi akewo, kenaka inakhala pa mpando wake waufumu. Iye anayitanitsa mpando wina kuti amayi ake akhalepo ndipo anakhala pansi ku dzanja lake lamanja.
Amayi akewo anati, “Ndikufuna ndikupempheni kanthu kakangʼono. Chonde musandikanize.”
Mfumu inayankha kuti, “Pemphani amayi, ine sindikukanizani.”
Ndipo amayiwo anati, “Mulole kuti Abisagi wa ku Sunemu akhale mkazi wa mʼbale wanu Adoniya.”
Koma Mfumu Solomoni inayankha amayi ake aja kuti, “Chifukwa chiyani mukupemphera Adoniya Abisagi wa ku Sunemu? Mungathenso kumupemphera ufumu pakuti iyeyu ndi mkulu wanga ndipo mupemphereninso wansembe Abiatara ndi Yowabu mwana wa Zeruya!”
Pamenepo Mfumu Solomoni inalumbira mʼdzina la Yehova kuti, “Mulungu andilange ine koopsa ngati Adoniya saphedwa chifukwa cha pempho lakeli! Tsono pali Yehova wamoyo, amene anandikhazikitsa ine pa mpando waufumu wa abambo anga Davide ndi kundipatsa ufumu monga analonjezera, Adoniya aphedwa lero lomwe lino!” Choncho Mfumu Solomoni inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo anakantha Adoniyayo, nafa.
Ndipo mfumu inati kwa Abiatara wansembe, “Pita ku Anatoti ku minda yako chifukwa ndiwe woyenera kufa, koma sindikupha tsopano, chifukwa unkanyamula Bokosi la Chipangano la Ambuye Yehova pamaso pa abambo anga Davide ndipo unazunzika limodzi ndi abambo angawo.” Kotero Solomoni anachotsa Abiatara pa udindo wokhala wansembe wa Yehova, kukwaniritsa mawu a Yehova amene anayankhula za nyumba ya Eli ku Silo.
Yowabu atamva zimenezi anathawira ku tenti ya Yehova ndipo anakagwira msonga za guwa lansembe, popeza Yowabu ndiye anathandiza Adoniya kuwukira koma sanathandize Abisalomu. Mfumu Solomoni inawuzidwa kuti Yowabu wathawira ku tenti ya Yehova ndipo ali pambali pa guwa lansembe. Tsono Solomoni analamula Benaya mwana wa Yehoyada kuti, “Pita, kamukanthe!”
Choncho Benaya analowa mʼtenti ya Yehova ndipo anati kwa Yowabu, “Mfumu ikuti ‘Tuluka!’ ”
Koma iye anayankha kuti, “Ayi, ine ndifera muno.”
Benaya anakafotokozera mfumu kuti, “Umu ndi mmene Yowabu wandiyankhira.”
Pamenepo mfumu inalamula Benaya kuti, “Kachite monga iye wanenera. Ukamukanthe ndi kumuyika mʼmanda. Ukatero udzandichotsera ine pamodzi ndi nyumba ya abambo anga mlandu wa anthu osalakwa amene Yowabu anawapha. Yehova adzamubwezera zomwe anachita pokhetsa magazi, chifukwa iye anakantha ndi lupanga anthu awiri abwino ndi olungama kuposa iye, nawapha, abambo anga Davide osadziwa. Anthu awiriwo ndi Abineri mwana wa Neri, wolamulira gulu lankhondo la Israeli ndi Amasa mwana wa Yeteri, wolamulira gulu lankhondo la Yuda. Magazi amene Yowabu anakhetsa akhale pamutu pake ndi pa zidzukulu zake kwamuyaya. Koma pa Davide ndi zidzukulu zake, nyumba yake ndi mpando wake waufumu pakhale mtendere wochokera kwa Yehova kwamuyaya.”
Choncho Benaya mwana wa Yehoyada anapita kukakantha Yowabu nʼkumupha ndipo anayikidwa mʼmanda mʼnyumba yakeyake ya ku chipululu. Mfumu inayika Benaya mwana wa Yehoyada kuti akhale woyangʼanira gulu lankhondo mʼmalo mwa Yowabu ndipo inayika Zadoki kuti akhale wansembe mʼmalo mwa Abiatara.
Kenaka mfumu inatuma anthu kukayitana Simei ndipo inamuwuza kuti, “Udzimangire nyumba mu Yerusalemu ndipo uzikhala kumeneko, koma usatuluke mu mzinda kupita kwina kulikonse. Tsiku lomwe udzatulukemo ndi kuwoloka Chigwa cha Kidroni, udziwiretu kuti udzafa ndipo magazi ako adzakhala pamutu pako.”
Simei anayankha mfumu kuti, “Zimene mwanenazi nʼzabwino. Kapolo wanu adzachita monga mbuye wanga mfumu mwanenera.” Choncho Simei anakhala mu Yerusalemu nthawi yayitali.
Koma patatha zaka zitatu, akapolo awiri a Simei anathawira kwa Akisi mwana wa Maaka, mfumu ya ku Gati, ndipo Simei anawuzidwa kuti, “Akapolo anu ali ku Gati.” Atamva zimenezi, anakwera bulu wake ndipo anapita kwa Akisi ku Gati kukafunafuna akapolo ake. Choncho Simei anapita ndi kukatenga akapolo ake ku Gati ndipo anabwera nawo.
Solomoni atawuzidwa kuti Simei anatuluka mu Yerusalemu ndi kupita ku Gati ndipo kuti wabwerako, mfumu inamuyitanitsa Simei ndipo inamufunsa kuti, “Kodi sindinakulumbiritse mʼdzina la Yehova ndi kukuchenjeza kuti, ‘Tsiku limene udzatuluka kupita kwina kulikonse, udziwe kuti udzafa’? Nthawi imeneyo iwe unandiwuza kuti, ‘Zimene mwanena nʼzabwino. Ine ndidzamvera.’ Chifukwa chiyani tsono sunasunge lumbiro lako kwa Yehova? Bwanji nanga sunamvere lamulo limene ndinakuwuza?”
Mfumuyo inawuzanso Simei kuti, “Ukudziwa mu mtima mwakomo zoyipa zonse zimene unachitira abambo anga Davide. Tsopano Yehova akubwezera zoyipa zakozo. Koma Mfumu Solomoni idzadalitsidwa ndipo mpando waufumu wa Davide udzakhazikika pamaso pa Yehova kwamuyaya.”
Pamenepo mfumu inalamula Benaya mwana wa Yehoyada ndipo iye anapita kukakantha Simei ndi kumupha.
Tsono ufumu unakhazikika mʼdzanja la Solomoni.
Solomoni Apempha Nzeru
Solomoni anachita ubale ndi Farao mfumu ya ku Igupto ndipo anakwatira mwana wake wamkazi. Mkaziyo anabwera naye mu Mzinda wa Davide mpaka anatsiriza kumanga nyumba yaufumu ndi Nyumba ya Yehova ndiponso khoma lozungulira Yerusalemu. Koma anthu ankaperekabe nsembe ku malo achipembedzo osiyanasiyana chifukwa chakuti mpaka pa nthawi imeneyo Dzina la Yehova anali asanalimangire nyumba. Solomoni anaonetsa chikondi chake pa Yehova poyenda motsatira malamulo a abambo ake Davide, kupatula kuti ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani ku malo osiyanasiyana achipembedzo.
Mfumu inapita ku Gibiyoni kukapereka nsembe popeza kumeneko ndiye kunali malo oposa malo ofunika kwambiri pachipembedzo. Kumeneko Solomoni anapereka nsembe zopsereza 1,000 pa guwa lansembe. Ku Gibiyoniko Yehova anaonekera kwa Solomoni mʼmaloto usiku, ndipo Mulungu anati, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.”
Solomoni anayankha kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa kapolo wanu, abambo anga Davide, chifukwa anali wokhulupirika pamaso panu, wolungama mtima ndiponso wa mtima wangwiro. Inu mukupitirizabe kukoma mtima kwanu kwakukulu kwa iye ndipo mwamupatsa mwana kuti akhale pa mpando wake waufumu lero lino.
“Tsopano Inu Yehova Mulungu wanga, mtumiki wanune mwandiyika kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo anga Davide. Komatu ndine mwana wamngʼono ndipo sindidziwa kagwiridwe kake ka ntchito yangayi. Mtumiki wanu ali pakati pa anthu amene munawasankha, mtundu waukulu, anthu ochuluka kwambiri osatheka kuwawerenga. Choncho mupatseni mtumiki wanu nzeru zolamulira anthu anu ndi kuti azitha kusiyanitsa pakati pa chabwino ndi choyipa. Pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?”
Ambuye anakondwera kuti Solomoni anapempha zimenezi. Tsono Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza wapempha zinthu zimenezi osati moyo wautali kapena chuma chako kapena imfa ya adani ako koma nzeru zolamulira anthu mwachilungamo, Ine ndidzakuchitira zimene wapempha. Ndidzakupatsa mtima wanzeru ndi wozindikira zinthu, kotero kuti sipanakhalepo wina wofanana nawe ndipo sipadzapezekanso wina wonga iwe pambuyo pako. Kuwonjeza apo, ndidzakupatsa zimene sunazipemphe: chuma ndi ulemu, kotero kuti pa masiku onse a moyo wako sipadzakhala mfumu yofanana nawe. Ndipo ngati udzayenda mʼnjira zanga ndi kumvera malamulo anga ndiponso malangizo anga monga abambo ako Davide anachitira, ndidzakupatsa moyo wautali.” Kotero Solomoni anadzuka ndipo anazindikira kuti anali maloto.
Iye anabwerera ku Yerusalemu nakayimirira patsogolo pa Bokosi la Chipangano la Ambuye ndipo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Kenaka anakonzera phwando atumiki ake onse.
Kuweruza Kolungama
Nthawi ina amayi awiri adama anabwera kwa mfumu ndipo anayima pamaso pake. Mmodzi mwa amayiwo anati, “Mbuye wanga, mayi uyu ndi ine timakhala nyumba imodzi. Ine ndinabala mwana tili limodzi ndi mnzangayu. Tsiku lachitatu ine nditabala mwana, mnzangayunso anabereka mwana wake. Tinalipo awiriwiri mʼnyumbamo ndipo munalibe wina aliyense.
“Nthawi ya usiku mwana wa mnzangayu anafa chifukwa anamugonera. Tsono iyeyu anadzuka pakati pa usiku, natenga mwana wanga ku mimba kwanga pamene ine mdzakazi wanu ndinali mʼtulo. Anamuyika mwanayo ku mimba kwake ndi kuyika mwana wake wakufayo ku mimba kwanga. Mmawa nditadzuka kuti ndiyamwitse mwana wanga ndinapeza kuti ndi wakufa! Koma kutacha nditamuyangʼanitsitsa ndinaona kuti si mwana amene ine ndinabala.”
Koma mayi winayo anati, “Ayi! Mwana wamoyoyu ndi wanga, mwana wakufayu ndi wako.”
Koma mayi woyambayo analimbikira kuti. “Ayi! Mwana wakufayu ndi wako; wamoyoyu ndi wanga.” Motero akaziwa anatsutsana pamaso pa mfumu.
Pamenepo mfumu inati, “Wina akuti, ‘Mwana wanga ndi wamoyoyu ndipo mwana wako ndi wakufayu,’ pamene winanso akuti, ‘Ayi! Mwana wako ndi wakufayu wanga ndi wamoyoyu.’ ”
Pamenepo mfumu inati, “Patseni lupanga.” Ndipo anabwera nalo lupanga kwa mfumu. Tsono mfumu inagamula kuti, “Muduleni pakati mwana wamoyoyu ndipo wina mumupatse gawo limodzi, gawo linalo mumupatse winayo.”
Mayi amene mwana wake anali moyo anagwidwa ndi chisoni chifukwa cha mwana wakeyo ndipo anawuza mfumu kuti, “Chonde mbuye wanga, mupatseni mnzangayu mwana wamoyoyu! Musamuphe!”
Koma winayo anati, “Ayi, asandipatse ine kapena iwe. Muduleni pakati!”
Choncho mfumu inagamula kuti, “Perekani mwana wamoyoyu kwa mayi woyambayu. Musamuphe, iyeyu ndiye mayi wake wa mwanayu.”
Pamene Aisraeli onse anamva za chigamulo chimene mfumu inapereka, anaopa mfumuyo kwambiri, chifukwa anaona kuti mfumu inali ndi nzeru zochokera kwa Mulungu zoweruzira mwachilungamo.
Nduna za Solomoni ndi Abwanamkubwa
Ndipo Mfumu Solomoni inakhala mfumu ya Aisraeli onse. Nduna zake zikuluzikulu zinali izi:
Azariya mwana wa Zadoki anali wansembe;
Elihorefe ndi Ahiya, ana a Sisa, anali alembi;
Yehosafati mwana wa Ahiludi, anali mlembi wa zochitika;
Benaya mwana wa Yehoyada, anali mtsogoleri wa ankhondo;
Zadoki ndi Abiatara, anali ansembe;
Azariya mwana wa Natani, anali woyangʼanira nduna za mʼzigawo;
Zabudi mwana wa Natani, anali wansembe ndi bwenzi la mfumu;
Ahisara, anali mkulu woyangʼanira nyumba ya mfumu;
Adoniramu mwana wa Abida, anali mkulu woyangʼanira ntchito za thangata.
Solomoni analinso ndi abwanamkubwa khumi ndi awiri amene ankayangʼanira zigawo zonse za dziko la Israeli. Iwo ankapereka chakudya kwa mfumu ndiponso ku banja laufumu. Bwanamkubwa aliyense ankapereka chakudya mwezi umodzi pa chaka. Mayina awo ndi awa:
Beni-Huri, wa ku dziko la mapiri la Efereimu;
Beni-Dekeri, woyangʼanira mizinda ya Makazi, Saalibimu, Beti-Semesi ndi Eloni Beti-Hanani;
Beni-Hesedi, woyangʼanira mizinda ya Aruboti (Soko ndi dziko lonse la Heferi);
Beni-Abinadabu, woyangʼanira Nafoti Dori (iye anakwatira Tafati mwana wa Solomoni);
Baana mwana wa Ahiludi, anali woyangʼanira Taanaki ndi Megido, ndi ku Beti Sani konse, kufupi ndi ku Zaretani kumunsi kwa Yezireeli, kuyambira ku Beti-Seani mpaka ku Abeli-Mehola kukafika mpaka ku Yokineamu;
Beni-Geberi, anali woyangʼanira Ramoti Giliyadi (midzi ya Yairi inali ya mwana wa Manase ku Giliyadi, pamodzinso ndi chigawo cha Arigobu ku Basani ndiponso mizinda yake yayikulu makumi asanu ndi umodzi yokhala ndi malinga ndi mipiringidzo yamkuwa).
Ahinadabu mwana wa Ido, anali woyangʼanira Mahanaimu;
Ahimaazi anali woyangʼanira Nafutali (iyeyu anakwatira Basemati mwana wa Solomoni);
Baana mwana wa Husai, anali woyangʼanira Aseri ndi Bealoti;
Yehosafati mwana wa Paruwa, anali woyangʼanira Isakara;
Simei mwana wa Ela, anali woyangʼanira Benjamini;
Geberi mwana wa Uri, anali woyangʼanira Giliyadi (dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi mfumu ya Basani). Iye ankayangʼanira chigawo chonsechi yekha.
Chakudya cha Tsiku ndi Tsiku cha Solomoni
Anthu a ku Yuda ndi ku Israeli anali ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Ankadya ndi kumwa ndipo ankasangalala. Ndipo Solomoni analamulira mayiko onse kuyambira ku mtsinje wa Yufurate mpaka ku dziko la Afilisti, kukafika mpaka ku malire a dziko la Igupto. Mayikowa ankabweretsa mphatso ndipo anali pansi pa ulamuliro wa Solomoni moyo wake wonse.
Chakudya cha tsiku ndi tsiku cha Solomoni chinali madengu 150 a ufa wosalala ndi madengu 300 a mgayiwa, ngʼombe khumi zonenepa zodyetsera mʼkhola, ngʼombe za ku busa makumi awiri, ndiponso nkhosa ndi mbuzi 100, pamodzinso ndi mbawala, agwape, mphoyo ndi mbalame zoweta zonona. Pakuti ankalamulira dziko lonse la kumadzulo kwa mtsinje wa Yufurate kuyambira ku Tifisa mpaka ku Gaza, mafumu onse a kumadzulo kwa Mtsinje, ndipo anali pa mtendere ndi mayiko onse ozungulira. Pa nthawi ya Solomoni, Yuda ndi Israeli anali pa mtendere, kuyambira ku Dani mpaka ku Beeriseba. Munthu aliyense ankangodzikhalira pansi pa mpesa wake ndi mtengo wake wa mkuyu.
Solomoni anali ndi zipinda 4,000 zodyeramo akavalo okoka magaleta ake ndi anthu 12,000 oyendetsa magaleta.
Abwanamkubwa a zigawo aja, aliyense pa mwezi wake, ankapereka chakudya cha Mfumu Solomoni ndi cha anthu onse amene ankadya naye. Iwo ankaonetsetsa kuti pasasowe kalikonse. Ankabweretsanso ku malo ake ofunikira muyeso wawo wa barele ndi udzu wa akavalo okoka magaleta ndiponso akavalo ena.
Nzeru za Solomoni
Mulungu anamupatsa Solomoni nzeru ndi luntha losaneneka ndipo nzeru zake zinali zochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. Nzeru za Solomoni zinali zoposa nzeru za anthu onse a Kummawa ndiponso nzeru zonse za ku Igupto. Iye anali wanzeru kuposa munthu wina aliyense, kuposa ngakhale Etani wa banja la Ezara, Hemani, Kalikoli ndi Darida, ana a Maholi. Ndipo mbiri yake inamveka kwa mitundu yonse ya anthu ozungulira. Solomoni anapeka miyambi 3,000 ndi kulemba nyimbo 1,005. Iye ankaphunzitsa za mitengo, kuyambira mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni mpaka kachitsamba ka hisope khomera pa khoma. Iye ankaphunzitsanso za nyama ndi mbalame, zinthu zokwawa pansi ndiponso za nsomba. Anthu a mitundu yonse ankabwera kudzamva nzeru za Solomoni. Anthu amenewa ankatumizidwa ndi mafumu onse a dziko lapansi amene anamvapo za nzeru zakezo.
Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu
Hiramu mfumu ya ku Turo atamva kuti Solomoni wadzozedwa kukhala mfumu mʼmalo mwa abambo ake Davide, anatumiza akazembe ake kwa Solomoni, chifukwa mfumu Hiramu inali pa ubale wabwino ndi Davide nthawi zonse. Solomoni anabweza mawu awa kwa Hiramu:
“Inu mukudziwa kuti chifukwa cha nkhondo zimene zinkachokera ku mbali zonse kulimbana ndi abambo anga, iwo sanathe kumangira Nyumba Yehova Mulungu wawo, mpaka Yehova atawayika adani awo pansi pa ulamuliro wawo. Koma tsopano Yehova Mulungu wanga wandipatsa mtendere mbali zonse za dziko ndipo ndilibe mdani kapena chovuta chilichonse. Choncho ine ndikufuna kumangira nyumba Yehova Mulungu wanga, monga momwe Iye anawuzira abambo anga Davide kuti, ‘Mwana wako amene ndidzamukhazike pa mpando waufumu mʼmalo mwako ndiye adzandimangire Nyumba.’
“Choncho lamulani kuti andidulire mikungudza ya ku Lebanoni. Anthu anga adzagwira ntchito imeneyo pamodzi ndi anthu anuwo, ndipo ine ndidzalipira anthu anuwo malipiro amene inu mungakhazikitse. Inu mukudziwa kuti ife tilibe anthu aluso locheka matabwa monga Asidoni.”
Hiramu anakondwa kwambiri atamva uthenga wa Solomoni ndipo anati, “Lero Yehova atamandike chifukwa wapatsa Davide mwana wanzeru kuti alamulire mtundu waukuluwu.”
Tsono Hiramu anabweza mawu awa kwa Solomoni:
“Ndalandira uthenga umene mwanditumizira ndipo ine ndidzachita zonse zimene mukufuna pokupatsani mitengo ya mkungudza ndi payini. Anthu anga adzatsika nayo kuchokera ku Lebanoni mpaka ku nyanja, ndipo adzayiyandamitsa pa nyanja mpaka ku malo amene munene. Kumeneko ndidzayimasula ndipo mudzayitenga. Ndipo inu mudzakwaniritsa chokhumba changa pondipatsa chakudya cha banja langa laufumu.”
Motero Hiramu anapereka kwa Solomoni mitengo yonse ya mkungudza ndi payini imene ankayifuna, ndipo Solomoni anamupatsa Hiramu mitanga ya tirigu 20,000 ngati chakudya cha pa nyumba yake, kuwonjezera pa migolo ya mafuta a olivi yokwana 20,000. Solomoni anapitiriza kupereka zimenezi chaka ndi chaka. Yehova anamupatsa Solomoni nzeru monga momwe analonjezera. Panali ubale wa mtendere pakati pa Solomoni ndi Hiramu, ndipo awiriwa anachita pangano.
Mfumu Solomoni inasonkhanitsa anthu ogwira ntchito ya thangata mʼdziko lonse la Israeli ndipo anthu athangatawo analipo 30,000. Iye ankatumiza anthu 10,000 ku Lebanoni pa mwezi mosinthanasinthana, kotero kuti ankakhala ku Lebanoniko mwezi umodzi ndipo kwawo ankakhalako miyezi iwiri. Adoniramu ndiye ankayangʼanira ogwira ntchito yathangatayo. Solomoni anali ndi anthu amtengatenga 70,000, anthu 80,000 osema miyala ku mapiri, ndi akapitawo 33,000 amene ankayangʼanira ntchitoyi ndiponso anthu ogwira ntchito zina. Molamulidwa ndi mfumu, anakumba ndi kusema miyala ikuluikulu kwambiri yoti akamangire maziko a Nyumba ya Mulungu. Amisiri a Solomoni ndi a Hiramu ndiponso anthu a ku Gebala anasema miyala ndi kukonza matabwa ndi miyala yomangira Nyumba ya Mulungu.
Solomoni Amanga Nyumba ya Mulungu
Patapita zaka 480 Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto, chaka chachinayi cha ulamuliro wa Solomoni mu Israeli, mwezi wa Zivi, umene ndi mwezi wachiwiri, Solomoni anayamba kumanga Nyumba ya Yehova.
Nyumba imene Solomoni anamangira Yehova mulitali mwake inali mamita 27, mulifupi mwake inali mamita asanu ndi anayi, ndipo msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. Chipinda chakubwalo mʼmbali mwake chinali mamita asanu ndi anayi kulingana ndi mulifupi mwa Nyumbayo ndipo kutalika kwake kunali kwa mamita anayi ndi theka. Anapanga mazenera amene maferemu ake anali olowa mʼkati mwa makoma a Nyumbayo. Mʼmbali mwa makoma a Nyumba yayikulu ndi chipinda chopatulika chamʼkati, anamanga zipinda zosanjikizana, mozungulira. Chipinda chapansi, mulifupi mwake chinali mamita awiri, chipinda chapakati mulifupi mwake chinali mamita awiri ndi theka ndipo chipinda chapamwamba penipeni mulifupi mwake chinali mamita atatu. Iye anapanga zinthu zosongoka kunja kwa khoma la kunja kuzungulira Nyumbayo kuti asamapise kanthu pa makoma a Nyumba ya Mulungu.
Poyimanga Nyumbayo, anagwiritsa ntchito miyala yosemeratu, ndipo pogwira ntchitoyo sipanamveke nyundo, nkhwangwa kapena chida china chilichonse.
Chipata cholowera ku chipinda chapansi chinali mbali ya kummwera kwa Nyumbayo. Panali makwerero okwerera ku chipinda chapakati ndiponso chipinda cha pamwamba. Choncho anamanga Nyumbayo mpaka kuyimaliza ndipo denga lake linali la mitanda ndi matabwa a mkungudza. Msinkhu wa chipinda chilichonse unali mamita awiri, ndipo anazilumukiza ku Nyumbayo ndi mitanda yamkungudza.
Yehova anayankhula ndi Solomoni kuti, “Kunena za Nyumba imene ukumangayi, ngati iwe udzamvera malangizo anga ndi kutsatira mawu anga, ngati udzasunga malamulo anga ndi kuwachita, Ine ndidzakwaniritsa zonse zomwe ndinalonjeza Davide abambo ako. Ndipo Ine ndidzakhazikika pakati pa ana a Israeli ndipo sindidzawasiya anthu anga Aisraeli.”
Kotero Solomoni anamanga Nyumba ya Mulungu nayimaliza. Anakuta khoma la mʼkati mwake ndi matabwa a mkungudza, kuyambira pansi pa Nyumbayo mpaka ku denga ndipo pansi pa Nyumbayo anayalapo matabwa a payini. Kumbuyo kwa Nyumbayo anadula chipinda chachitali mamita asanu ndi anayi. Chipindachi anachimanga ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka ku denga kuti chikhale chipinda chopatulika chamʼkati mwa Nyumba ya Mulungu ngati Malo Wopatulika Kwambiri. Chipinda chachikulu chimene chinali kutsogolo kwa Malo Wopatulika Kwambiriwa, chinali mamita 18 mulitali mwake. Mʼkati mwa Nyumbayi munali matabwa a mkungudza, pamene anajambulapo zithunzi za zikho ndi maluwa. Paliponse panali mkungudza wokhawokha. Panalibe mwala uliwonse umene unkaonekera.
Anakonza malo wopatulika mʼkati mwa Nyumbayi kuti ayikemo Bokosi la Chipangano cha Yehova. Malo wopatulika a mʼkatiwo anali a mamita asanu ndi anayi mulitali mwake, mulifupi mwake, ndi msinkhu wake. Anakuta mʼkati mwake ndi golide weniweni ndiponso anapanga guwa lansembe la matabwa a mkungudza. Solomoni anakutira golide weniweni mʼkati mwake mwa Nyumbayi, ndipo anayalika maunyolo a golide mopingasa kutsogolo kwa malo wopatulika amene anakutidwa ndi golide. Motero anakuta mʼkati monse ndi golide. Anakutanso ndi golide guwa lansembe la mʼkati mwa chipinda chopatulika.
Mʼchipinda chopatulika cha mʼkati anapangamo akerubi awiri a mtengo wa olivi. Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka. Phiko limodzi la kerubi kutalika kwake kunali mamita awiri ndi theka, phiko linanso linali mamita awiri ndi theka, kutambasula mapiko awiriwo, kuchokera msonga ina mpaka msonga ina kutalika kwake kunali mamita anayi ndi theka. Kerubi wachiwiriyo msinkhu wake unalinso mamita anayi ndi theka, pakuti akerubi awiriwo anali a misinkhu yofanana ndi a mapangidwe ofanana. Msinkhu wa kerubi aliyense unali mamita anayi ndi theka. Solomoni anayika akerubiwo mʼchipinda cha mʼkati mwenimweni mwa Nyumba ya Mulungu, atatambasula mapiko awo. Phiko la kerubi wina limakhudza khoma lina, pamene phiko la winayo limakhudza khoma linanso ndipo mapiko awo amakhudzana pakati pa chipindacho. Akerubiwo anawakuta ndi golide.
Pa makoma onse kuzungulira Nyumbayo, mʼzipinda za mʼkati ndi za kunja zomwe, anajambulapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa. Anayala golide pansi mu Nyumbamo mʼzipinda zamʼkati ndi zakunja zomwe.
Ndipo pa khomo lolowera ku malo wopatulika amʼkati anapanga zitseko za mtengo wa olivi ndipo khonde lake linali ndi mbali zisanu. Ndipo pa zitseko ziwiri zija za mtengo wa olivi anajambulapo kerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa ndipo anapaka golide akerubiwo ndi mitengo ya mgwalangwayo. Anapanganso chimodzimodzi mphuthu za mbali zinayi za mtengo wa olivi za pa khomo la Nyumbayo. Solomoni anapanganso zitseko ziwiri za payini. Chitseko chilichonse chinali ndi mbali ziwiri zotha kuzipinda. Pa zitsekozo anagobapo akerubi, mitengo ya mgwalangwa ndi maluwa wotambasuka ndipo zojambulazo anazikuta ndi golide wopyapyala.
Ndipo anamanga bwalo la mʼkati lokhala ndi khoma lokhala ndi mizere itatu ya miyala yosema ndiponso mzere umodzi wa matabwa osemedwa a mkungudza.
Maziko a Nyumba ya Yehova anamangidwa pa chaka chachinayi, mwezi wa Zivi. Pa chaka cha 11 mwezi wa Buli, mwezi wachisanu ndi chitatu, madera onse a Nyumba anatha kumangidwa monga momwe kunkafunikira. Anamanga Nyumbayo kwa zaka zisanu ndi ziwiri.
Solomoni Amanga Nyumba Yake Yaufumu
Solomoni anamanga nyumba yake yaufumu kwa zaka 13. Iye anamanga nyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni yomwe mulitali mwake inali mamita 44, mulifupi mwake mamita 22, msinkhu wake mamita 13 ndi theka; ndipo inakhazikika pa mizere inayi ya mapanda a mkungudza yokhala ndi mitanda ya mkungudza yotanthalika pa mapandawo. Pamwamba pa mitandapo panali matabwa a mkungudza amene anaphimba zipinda zimene zinamangidwa pa nsanamira 45, pa mzere uliwonse nsanamira 15. Mazenera a nyumbayo anali mmwamba mʼmizere itatu, zenera kuyangʼanana ndi zenera linzake. Zitseko zonse ndi mazenera omwe, maferemu ake anali ofanana mbali zonse. Mulitali mwake ndi mulifupi mwake, ndipo zenera linkapenyana ndi zenera linzake pa mizere itatu.
Iye anapanga Chipinda cha Nsanamira. Mulitali mwake munali mamita 22, mulifupi mwake munali mamita 13 ndi theka. Patsogolo pake panali khonde ndi nsanamira zokhala ndi denga.
Anamanga chipinda cha mpando waufumu, Chipinda cha Chilungamo, modzaweruziramo milandu ndipo anayikutira ndi matabwa a mkungudza kuchokera pansi mpaka ku denga. Ndipo nyumba yake yodzakhalamo anayimanga kumbuyo kwa chipindacho. Nyumbayo anayimanga mofanana ndi Chipindacho. Solomoni anamanga nyumba inanso yofanana ndi chipindachi, kumangira mkazi wake mwana wa Farao.
Nyumba zonsezi, kuyambira kunja mpaka ku bwalo lalikulu ndiponso kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, zinapangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene anayisema potengera miyeso yake yoyenera ndipo anayisalaza ndi macheka mʼkati ndi kunja komwe. Maziko ake anali a miyala yabwino kwambiri, kutalika kwa miyala ina kunali mamita atatu ndi theka, inanso mamita anayi. Pamwamba pake panali pa miyala yabwino kwambiri, yosemedwa potengera miyeso yake. Pamwamba pa miyalayo panali matabwa a mkungudza. Bwalo lalikulu lozungulira nyumbayi linali ndi khoma la mizere itatu ya miyala yosemedwa ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza. Bwalo la mʼkati la Nyumba ya Yehova ndiponso khonde lake anazimanga mofanana.
Zipangizo za mʼNyumba ya Mulungu
Mfumu Solomoni anatuma anthu ku Turo ndipo anakabwera ndi Hiramu, mwana wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali ndipo abambo ake anali a ku Turo, mʼmisiri wa mkuwa. Hiramu anali munthu wa luso lalikulu ndiponso wodziwa kupanga zinthu za mkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomoni ndi kugwira ntchito zonse zimene anamupatsa.
Iye anawumba nsanamira ziwiri za mkuwa, nsanamira iliyonse msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu ndipo thunthu lake akazunguliza chingwe, linali mamita asanu ndi theka. Anapanganso mitu iwiri ya mkuwa ndi kuyiika pamwamba pa nsanamira zija; mutu uliwonse unali wotalika kupitirirapo mamita awiri. Pa mitu ya pa nsanamirazo anakolekapo maunyolo awiri olukanalukana ndi oyangayanga. Mutu uliwonse unali ndi maunyolo oterewa asanu ndi awiri. Anapanga mizere iwiri ya zinthu zonga makangadza mozungulira pamwamba pa maunyolo kukongoletsa mitu ya nsanamirazo. Anachita chimodzimodzi ndi mutu uliwonse. Mitu imene inali pamwamba pa nsanamira mʼkhonde inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Kutalika kwake kunali pafupifupi mamita awiri. Pa mitu yonse iwiri ya pamwamba pa nsanamira, pamwamba pa chigawo chonga mʼphika pafupi ndi cholukidwa ngati ukonde, panali makangadza 200 okhala mozungulira mʼmizere. Anayimika nsanamirazo pa khonde la Nyumba ya Mulungu. Nsanamira ya kumpoto anayitcha Yakini ndipo ya kummwera anayitcha Bowazi. Mitu ya pamwamba pa nsanamirazo inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Motero anamaliza ntchito ya nsanamirazo.
Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13. Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo tizikho kuzungulira thunthu lonse la mbiyayo, tizikho khumi pa theka la mita. Tizikhoto tinali mʼmizere iwiri ndipo anatipangira kumodzi ndi mbiyayo.
Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati. Mbiyayo inali yonenepa ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 40,000.
Iye anapanganso maphaka khumi a mkuwa. Phaka lililonse mulitali mwake linali pafupifupi mamita awiri, mulifupi mwake linali pafupifupi mamita awiri, ndipo msinkhu wake unali kupitirirapo mita imodzi. Maphakawo anapangidwa motere: Anali ndi matabwa a mʼmbali amene ankalowa mʼmaferemu. Pakati pa matabwa a mʼmbali ndi maferemu panali zithunzi za mikango, ngʼombe zazimuna ndi akerubi. Pa maferemuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ngʼombe zazimunazo anajambulapo nkhata za maluwa. Phaka lililonse linali ndi mikombero ya mkuwa inayi ndi mitandanso ya mkuwa, ndipo phaka lililonse linali ndi zogwiriziza mbale zosambira pa ngodya zake zinayi, zopangidwa limodzi ndi nkhata za maluwa mbali zake zonse. Mʼkati mwa phakalo munali malo otsekuka amene anali ndi feremu yozungulira ndipo anali ozama theka la mita. Malo otsekukawa anali wozungulira, ndipo pamodzi ndi tsinde lake anali otalika masentimita 44. Kuzungulira pa malo otsekukawa panajambulidwa zokometsera. Matabwa oyimikira phakali anali ofanana mbali zonse, osati ozungulira. Pansi pa matabwawo panali mikombero inayi, ndipo mitanda ya mikomberoyo inalumikizidwa ku phakalo. Msinkhu wa mkombero uliwonse unali masentimita 66. Mikomberoyo inapangidwa ngati mikombero ya galeta; mitanda yake, marimu ake, sipokosi zake ndiponso mahabu ake, zonsezi zinali za chitsulo.
Phaka lililonse linali ndi zogwirira zinayi; chogwirira chimodzi pa ngodya iliyonse, zolumikizidwa ku phakalo. Pamwamba pa phakalo panali mkombero wozungulira ndipo msinkhu wake unali masentimita 22. Pamwamba pa phakalo panali zogwiriziza ndi matabwa ake, zolumikizidwa ku phakalo. Paliponse pamene panali malo woti nʼkujambulapo, pa zogwiriziza ndi pa matabwa, anagobapo zithunzi za akerubi, mikango ndi mitengo ya mgwalangwa. Anajambulanso nkhata za maluwa mozungulira. Umu ndi mmene anapangira maphaka khumiwo. Onse anawapanga malo ofanana ndipo anali a miyeso yofanana ndiponso wooneka mofanana.
Kenaka anapanga mabeseni akuluakulu khumi a mkuwa; beseni lililonse munkalowa madzi a malita 800, ndipo poyeza modutsa, pakamwa pake panali pafupifupi mamita awiri. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi beseni lake. Maphaka asanu anawayika mbali ya kummwera kwa Nyumba ya Mulungu, asanu enawo anawayika mbali ya kumpoto. Mbiyayo anayiyika mbali yakummwera, pa ngodya yakummwera cha kummawa kwa Nyumba ya Mulungu. Iye anapanganso miphika ndi mafosholo ndi mabeseni owazira magazi.
Kotero Hiramu anatsiriza ntchito yonse ya ku Nyumba ya Yehova imene ankagwirira Mfumu Solomoni:
nsanamira ziwiri;
mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;
maukonde awiri okongoletsera mbale ziwiri za mitu yapamwamba pa nsanamirazo;
makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);
maphaka khumi pamodzi ndi mabeseni khumi pa maphakawo;
mbiya pamodzi ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri zazimuna zosanjikapo mbiyayo;
miphika, mafosholo ndi mbale zowazira magazi.
Ziwiya zonsezi za ku Nyumba ya Yehova, zimene Hiramu anapangira Mfumu Solomoni, zinali zamkuwa wonyezimira. Mfumu inapangitsa zimenezi mʼchigwa cha Yorodani, ku malo amtapo amene anali pakati pa Sukoti ndi Zaretani. Solomoni sanayeze ziwiya zonsezi chifukwa zinali zambiri ndipo kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.
Solomoni anapanganso ziwiya zonse zimene zinali mʼNyumba ya Yehova:
guwa lansembe lagolide;
tebulo lagolide pamene ankayikapo buledi woperekedwa kwa Mulungu;
zoyikapo nyale zagolide weniweni (dzanja lamanja zisanu ndipo zisanu zina ku dzanja lamanzere, mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika);
maluwa agolide, nyale ndi mbaniro;
mbale zagolide weniweni, zozimitsira nyale, mbale zowazira magazi, mbale ndi zofukizira;
ndiponso zomangira zitseko zagolide za chipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndiponso za zitseko za chipinda chachikulu cha Nyumba ya Mulungu.
Pamene ntchito yonse imene Mfumu Solomoni inagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka: siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Yehova.
Abwera ndi Bokosi la Chipangano ku Nyumba ya Yehova
Pamenepo Mfumu Solomoni inasonkhanitsa akuluakulu a Israeli, atsogoleri onse a mafuko ndi akuluakulu a mabanja a Aisraeli mu Yerusalemu, kuti akatenge Bokosi la Chipangano la Yehova ku Ziyoni, Mzinda wa Davide. Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Mfumu Solomoni nthawi ya chikondwerero cha mwezi wa Etanimu, mwezi wachisanu ndi chiwiri.
Akuluakulu onse a Israeli atafika, ansembe ananyamula Bokosi la Chipangano, ndipo anabwera nalo Bokosi la Yehova pamodzi ndi tenti ya msonkhano ndi ziwiya zonse zopatulika zimene zinali mʼmenemo. Ansembe ndi Alevi ndiye anazinyamula, ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.
Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a akerubi. Akerubiwo anatambalitsa mapiko awo pamwamba pa Bokosi la Chipangano ndipo anaphimba bokosilo pamodzi ndi mitengo yonyamulira. Mitengoyi inali yayitali kwambiri ndipo inkaonekera kunja kwa chipinda chamʼkati cha Malo Opatulika koma osati kunja kwa Malo Opatulikawo; ndipo mitengoyi ilipo mpaka lero lino. Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
Ansembe atatuluka mʼMalo Opatulikawo, mtambo unadzaza Nyumba ya Yehova. Ndipo ansembewo sanathe kugwira ntchito yawo chifukwa cha mtambowo, pakuti ulemerero wa Yehova unadzaza mʼNyumba ya Yehova.
Pamenepo Solomoni anati, “Yehova anati adzakhala mʼmitambo yakuda; taonani ndithu, ine ndakumangirani Nyumba yokongola kwambiri, malo woti muzikhalamo mpaka muyaya.”
Aisraeli onse ali chiyimire pomwepo, mfumu inatembenuka ndi kuwadalitsa. Ndipo inati:
“Atamandike Yehova, Mulungu wa Israeli, amene wachita ndi dzanja lake zimene analonjeza ndi pakamwa pake kwa Davide abambo anga. Pakuti Iye anati, ‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisraeli ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba, koma ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisraeli.’
“Abambo anga Davide anali ndi maganizo mu mtima mwawo oti amangire nyumba Yehova, Mulungu wa Israeli. Koma Yehova ananena kwa abambo anga, Davide, kuti, ‘Popeza zinali mu mtima mwako kumangira nyumba Dzina langa, unachita bwino kukhala ndi maganizo amenewa mu mtima mwakomo. Komatu, si iwe amene udzamanga Nyumba ya Mulungu, koma mwana wako, mwana amene iwe udzabereke. Iyeyo ndiye adzandimangire Nyumba.’
“Yehova wasunga zimene analonjeza: ine ndalowa mʼmalo mwa abambo anga Davide ndipo tsopano ndili pa mpando waufumu wa Israeli, monga momwe Yehova analonjezera, ndipo ndamangira nyumba Dzina la Yehova, Mulungu wa Israeli. Ndalikonzera malo Bokosi la Chipangano mmene muli pangano la Yehova limene anapangana ndi makolo athu pamene anawatulutsa mʼdziko la Igupto.”
Pemphero Lodzipereka la Solomoni
Pamenepo Solomoni anayimirira patsogolo pa guwa lansembe la Yehova pamaso pa gulu lonse la Aisraeli ndipo anakweza manja ake kumwamba, nati:
“Inu Yehova, Mulungu wa Israeli, palibe Mulungu wofanana nanu kumwamba kapena pansi pa dziko, inu amene mumasunga pangano ndi kuonetsa chikondi chosasinthika kwa atumiki anu amene amayenda pamaso panu ndi mtima wawo wonse. Inu mwasunga lonjezo lanu kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu. Inde zimene munalonjeza ndi pakamwa panu, mwazikwaniritsa ndi manja anu, monga mmene tikuonera lero lino.
“Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu, pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo mokhulupirika monga iwe wachitira.’ Ndipo tsopano, Inu Mulungu wa Israeli, lolani kuti mawu anu akwaniritsidwe amene munalonjeza mtumiki wanu Davide abambo anga.
“Kodi Mulungu angakhaledi pa dziko lapansi? Mlengalenga ngakhale kumwamba kwenikweni, sikungakukwaneni. Nanga kuli bwanji ndi Nyumba iyi imene ndamanga! Koma Inu Yehova Mulungu wanga, imvani pemphero ndi pembedzero la mtumiki wanu. Imvani kulira ndi pemphero la mtumiki wanu limene ndikupempha pamaso panu lero lino. Maso anu azikhala otsekuka kuyangʼana Nyumba ino usiku ndi usana, malo ano amene Inu munanena kuti, ‘Dzina langa lidzakhala mʼmenemo,’ choncho imvani pemphero limene mtumiki wanu akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani pembedzero la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.
“Munthu akalakwira mnzake, nawuzidwa kuti alumbire, akabwera kudzalumbira patsogolo pa guwa lansembe la Nyumba ino, imvani kumwambako ndi kuchitapo kanthu. Weruzani atumiki anuwo, wochimwa mugamule kuti ndi wolakwa ndipo alangidwe chifukwa cha zimene wachita. Wosachimwa mugamule kuti ndi wosalakwa, ndipo muonetse kusalakwa kwakeko.
“Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani, ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera kwa Inu mʼNyumba ino, pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa makolo awo.
“Pamene kumwamba kwatsekeka ndipo mvula sikugwa chifukwa anthu anu akuchimwirani, ndipo pamene apemphera akuyangʼana malo ano ndi kuvomereza Dzina lanu, ndi kutembenuka kuchoka ku machimo awo chifukwa inu mwawalanga, pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.
“Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene mdani wazungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera, ndipo wina aliyense mwa Aisraeli akapemphera kapena kukudandaulirani, aliyense wa iwo akadziwa masautso a mu mtima mwake ndi kukweza manja awo kuloza Nyumba ino, pamenepo imvani kumwambako, malo anu wokhalamo. Khululukani ndipo chitanipo kanthu. Muchitire aliyense molingana ndi zonse zimene anachita, popeza inu mumadziwa mtima wake (pakuti ndinu nokha amene mumadziwa mitima ya anthu onse), motero iwo adzakuopani masiku onse amene adzakhale mʼdziko limene munalipereka kwa makolo athu.
“Ndipo kunena za mlendo amene si mmodzi wa anthu anu Aisraeli, koma wabwera kuchokera ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu, pakuti anthu adzamva za dzina lanu lotchukali ndiponso za dzanja lanu lamphamvu ndi lochita zazikulu, kudzapemphera akuyangʼana Nyumba ino, pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti Nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi Dzina lanu.
“Pamene anthu anu apita ku nkhondo kukamenyana ndi adani awo, kulikonse kumene mungawatume, ndipo pamene apemphera kwa Yehova moyangʼana mzinda umene mwausankha ndi Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu, imvani kumwambako pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo apambanitseni.
“Pamene akuchimwirani, popeza palibe munthu amene sachimwa, ndipo Inu nʼkuwakwiyira ndi kuwapereka kwa mdani, amene adzawatenga ukapolo kupita ku dziko lake, kutali kapena pafupi; ndipo ngati asintha maganizo ali ku dziko la ukapololo ndi kulapa ndi kukudandaulirani mʼdziko la owagonjetsa ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa, tachita zinthu zoyipa,’ ndipo ngati abwerera kwa Inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse mʼdziko la adani awo amene anawatenga ukapolo, ndi kupemphera kwa Inu moyangʼana dziko limene munapereka kwa makolo awo, moyangʼana mzinda umene munawusankha ndiponso Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu, imvani kumwambako, malo anu wokhalamo, imvani pemphero lawo ndi kudandaula kwawo, ndipo muwachitire zabwino. Ndipo khululukirani anthu anu amene akuchimwirani. Khululukirani zolakwa zonse akuchitirani ndipo mufewetse mitima ya amene anawagonjetsawo kuti awachitire chifundo; popeza ndi anthu anu ndiponso cholowa chanu, anthu omwe munawatulutsa ku Igupto, kuwachotsa mʼngʼanjo yamoto yosungunula zitsulo.
“Maso anu atsekuke kuti aone dandawulo la mtumiki wanu ndiponso madandawulo a anthu anu Aisraeli, ndipo mutchere khutu nthawi iliyonse pamene akulirirani. Pakuti Inu munawasiyanitsa ndi anthu a mitundu ina yonse ya dziko lonse kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munanenera kudzera mwa mtumiki wanu Mose pamene Inu, Ambuye Yehova, munatulutsa makolo athu ku Igupto.”
Solomoni atamaliza mapemphero ndi mapembedzero onsewa kwa Yehova, anayimirira pa guwa lansembe la Yehova, nagwada atakweza manja ake kumwamba. Anayimirira ndi kudalitsa gulu lonse la Aisraeli ndi mawu okweza, nati:
“Atamandike Yehova, amene wapereka mpumulo kwa anthu ake Aisraeli monga momwe analonjezera. Palibe mawu ndi amodzi omwe amene anapita pachabe pa malonjezo ake onse abwino amene anawapereka kudzera mwa mtumiki wake Mose. Yehova Mulungu wathu akhale nafe monga momwe anakhalira ndi makolo athu; asatisiye kapena kutitaya. Atembenuzire mitima yathu kwa Iye, kuti tiyende mʼnjira zake zonse ndi kusunga mawu ake, malamulo ake ndi malangizo ake amene anapereka kwa makolo athu. Ndipo mawu angawa, amene ndapemphera pamaso pa Yehova, asayiwalike pamaso pa Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, ndipo Iye alimbikitse mtumiki wake ndiponso athandize Aisraeli, anthu ake powapatsa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku, kotero kuti anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi adziwe kuti Yehova ndi Mulungu ndipo kuti palibenso wina. Koma mitima yanu ikhale yodzipereka kwathunthu kwa Yehova Mulungu wanu, kutsatira malamulo ake ndi kumvera malangizo ake, monga lero lino.”
Mwambo Wopereka Nyumba ya Mulungu
Ndipo mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapereka nsembe pamaso pa Yehova. Solomoni anapereka nsembe zachiyanjano kwa Yehova: ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapatula Nyumba ya Yehova.
Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo.
Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha ku Igupto. Anachita chikondwerero chimenechi pamaso pa Yehova Mulungu wathu kwa masiku asanu ndi awiri, anawonjezerapo masiku ena asanu ndi awiri, onse pamodzi ngati masiku 14. Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Solomoni anawuza anthu kuti apite kwawo. Anthuwo anathokoza mfumu ndipo kenaka anapita kwawo mokondwa ndi mosangalala mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira mtumiki wake Davide ndi anthu ake Aisraeli.
Yehova Aonekera Solomoni
Solomoni atatsiriza kumanga Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndi kukwaniritsa kuchita zonse zimene ankafuna, Yehova anamuonekera kachiwiri, monga momwe anamuonekera ku Gibiyoni. Yehova ananena kwa iye kuti:
“Ndamva pemphero ndi pembedzero lako pa zimene wapempha pamaso panga. Ndayipatula Nyumba iyi, imene wamanga, poyikamo Dzina langa mpaka muyaya. Maso anga ndi mtima wanga zidzakhala pamenepo nthawi zonse.
“Kunena za iwe, ukayenda pamaso panga mokhulupirika, mwangwiro ndi moona mtima monga momwe anachitira abambo ako Davide, ndi kuchita zonse zimene ndakulamula ndi kusamalitsa malangizo ndi malamulo anga, Ine ndidzakhazikitsa mpando wako waufumu pa Israeli mpaka muyaya, monga ndinalonjezera abambo ako Davide pamene ndinati, ‘Sipadzasowa munthu pa mpando waufumu wa Israeli.’
“Koma ngati iwe kapena ana ako mudzapatuka ndi kuleka kusunga malamulo ndi mawu anga amene ndakupatsani ndi kupita kukatumikira milungu ina ndi kuyipembedza, pamenepo Ine ndidzazula Aisraeli mʼdziko limene ndinawapatsa ndiponso ndidzayikana Nyumba ino imene ndayipatula chifukwa cha Dzina langa. Pamenepo Aisraeli adzasanduka mwambi ndi chinthu chonyozedwa pakati pa anthu onse. Ndipo ngakhale kuti tsopano Nyumba ya Mulunguyi ndi yokongola kwambiri, onse amene adzadutsa pano adzadabwa kwambiri ndipo adzatsonya ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachita chinthu chotere mʼdziko muno ndi pa Nyumba ya Mulunguyi?’ Anthu adzayankha kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti asiya Yehova Mulungu wawo amene anatulutsa makolo awo mʼdziko la Igupto, ndipo akangamira milungu ina ndi kumayipembedza ndi kuyitumikira. Choncho Iye wabweretsa zovuta zonsezi.’ ”
Zina zimene Solomoni Anachita
Patatha zaka makumi awiri, ndiye nthawi imene Solomoni anamanga nyumba ziwirizi: Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, Mfumu Solomoni anapereka mizinda makumi awiri ya ku Galileya kwa Hiramu mfumu ya ku Turo chifukwa Hiramu nʼkuti atapereka mitengo yonse ya mkungudza ndi ya payini ndiponso golide yense zimene Solomoni ankazifuna. Koma Hiramu atabwera kuchokera ku Turo kudzaona mizinda imene Solomoni anamupatsa, sanasangalatsidwe nayo mizindayo. Iye anafunsa kuti, “Mʼbale wanga, kodi iyi nʼkukhala mizinda yondipatsa?” Ndipo iye anayitcha mizindayo Dziko la Kabuli, dzina lomwe amatchedwa mpaka lero lino. Koma Hiramu anali atatumiza kwa mfumu golide oposa makilogalamu 4,000.
Izi ndi zimene anachita Mfumu Solomoni: Analamula anthu kuti agwire ntchito yathangata pomanga Nyumba ya Yehova, nyumba yake, malo achitetezo a Milo, mpanda wa Yerusalemu, Hazori, Megido ndi Gezeri. (Farao mfumu ya ku Igupto inali itathira nkhondo ndi kulanda Gezeri. Iye anatentha mzindawo. Anapha Akanaani amene ankakhala mʼmenemo ndipo kenaka anawupereka ngati mphatso yaukwati kwa mwana wake wamkazi amene anakwatiwa ndi Solomoni. Ndipo Solomoni anamanganso Gezeri.) Iye anamanga Beti-Horoni Wakumunsi, Baalati ndi Tadimori ku chipululu, mʼdziko lake lomwelo, pamodzinso ndi mizinda yake yosungira chuma ndiponso mizinda yosungiramo magaleta ndi akavalo ake. Anamanganso chilichonse chimene anafuna kumanga ku Yerusalemu, ku Lebanoni ndi ku madera onse amene iye ankalamulira.
Panali anthu amene anatsala pakati pa mitundu ya Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi (anthu awa sanali Aisraeli). Zimenezi ndiye zinali zidzukulu zawo zotsalira mʼdzikoli, anthu amene Aisraeli sanathe kuwawononga kotheratu. Solomoni anawatenga ndi kukhala akapolo ake ogwira ntchito yathangata, monga zilili mpaka lero lino. Koma Solomoni sanagwiritse ntchito ya ukapolo Mwisraeli aliyense; iwo anali anthu ake ankhondo, nduna zake, atsogoleri a ankhondo, akapitawo ake, olamulira magaleta ndi oyendetsa magaleta ake. Amenewa ndiwo anali akuluakulu oyangʼanira ntchito za Solomoni. Anthu okwana 550 ndiwo ankayangʼanira anthu amene ankagwira ntchitowo.
Mwana wamkazi wa Farao atachoka mu Mzinda wa Davide, kupita ku nyumba ya mfumu imene Solomoni anamumangira, Solomoni anamanga malo achitetezo a Milo.
Katatu pa chaka Solomoni ankapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pa guwa lansembe limene anamangira Yehova ndiponso ankafukiza lubani pamaso pa Yehova. Potero ankakwaniritsa zoyenera kuchitika mu Nyumba ya Yehova.
Mfumu Solomoni anapanganso sitima zapamadzi ku Ezioni Geberi, malo amene ali pafupi ndi Eloti ku Edomu, mʼmbali mwa Nyanja Yofiira. Ndipo Hiramu anatumiza anthu ake oyendetsa sitima zapamadzi amene ankadziwa za pa nyanja kuti aziyendetsa pamodzi ndi anthu a Solomoni. Iwo anapita ku Ofiri ndipo anakatenga golide okwana makilogalamu 14,000, amene anamupereka kwa Mfumu Solomoni.
Mfumu Yayikazi ya ku Seba Ibwera Kudzacheza ndi Solomoni
Mfumu yayikazi ya ku Seba itamva za kutchuka kwa Solomoni ndi za ubale wake ndi Yehova, inabwera kudzamuyesa ndi mafunso okhwima. Inafika mu Yerusalemu ndi gulu lalikulu la ngamira zonyamula zokometsera zakudya, golide wambiri ndi miyala yokongola. Inafika kwa Solomoni ndipo inayankhula naye zonse zimene zinali mu mtima mwake. Solomoni anayankha mafunso ake onse ndipo panalibe kanthu kalikonse kovuta komwe sanathe kufotokozera mfumu yayikaziyo. Mfumu yayikazi ya ku Seba itaona nzeru zonse za Solomoni ndiponso nyumba yaufumu imene anamanga, chakudya cha pa tebulo pake, moyo wa antchito ake ndi zovala zawo, atumiki opereka zakumwa, ndiponso nsembe zopsereza zimene ankapereka ku Nyumba ya Yehova, inathedwa nzeru.
Iyo inati kwa mfumu, “Mbiri imene ndinamva ndili ku dziko kwathu ya zomwe munachita komanso nzeru zanu ndi yoona. Koma sindinakhulupirire zinthu zimenezo mpaka nditafika ndi kuona ndi maso anga. Kunena zoona sanandiwuze ngakhale theka lomwe, pakuti nzeru ndi chuma zimene muli nazo zaposa zimene ndinamva. Ngodala anthu anu! Ngodala atumiki anu amene amayimirira pamaso panu nthawi zonse ndi kumamva nzeru zanu! Atamandike Yehova Mulungu wanu amene wakondwera nanu nakukhazikani pa mpando waufumu wa Israeli. Chifukwa cha chikondi chake chamuyaya pa Israeli, wayika inu kuti mukhale mfumu kuti mulamulire moyenera ndi mwachilungamo.”
Ndipo mfumu yayikaziyo inapatsa Solomoni golide wolemera makilogalamu 4,000, zokometsera zakudya zambirimbiri, ndiponso miyala yokongola. Sikunabwerenso zokometsera zakudya ngati zomwe mfumu yayikazi ya ku Seba inapatsa Mfumu Solomoni.
(Ndiponso sitima zapamadzi za Hiramu zinabweretsa golide wochokera ku Ofiri. Ndipo kuchokera kumeneko kunabweranso mitengo yambiri ya alimugi ndi miyala yokongola. Mfumu inagwiritsa ntchito mitengo ya alimugi ngati yochirikizira Nyumba ya Yehova ndi nyumba yaufumu, ndipo anapangiranso azeze ndi apangwe a anthu oyimba. Mitengo yotere sinayitanitsidweponso kapena kuoneka mpaka lero lino).
Mfumu Solomoni inapereka kwa mfumu yayikazi ya ku Seba zonse zimene inazifuna ndi kuzipempha, osawerengera mphatso zaufumu zimene anali atamupatsa. Choncho inabwerera ku dziko la kwawo pamodzi ndi atumiki ake.
Chuma ndi Ulemerero wa Solomoni
Golide amene Solomoni ankalandira pa chaka ankalemera makilogalamu 23,000, osawerengera misonkho imene anthu odzacheza ndi amalonda amapereka. Golide wina ankachokera kwa mafumu onse a ku Arabiya ndi kwa abwanamkubwa a mʼdzikomo.
Mfumu Solomoni anapanga zishango zikuluzikulu 200 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera makilogalamu atatu ndi theka. Anapanganso zishango zingʼonozingʼono 300 zagolide. Chishango chilichonse chimapangidwa ndi golide wolemera kilogalamu imodzi ndi theka. Ndipo mfumu inayika zishangozo mʼnyumba yake yotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya Lebanoni.
Mfumu inapangitsanso mpando waufumu waukulu wa minyanga ya njovu, ndipo inawukutira ndi golide wabwino kwambiri. Mpando waufumuwo unali ndi makwerero asanu ndi limodzi, ndipo chotsamira chake chinali chozungulira pamwamba pake. Mʼmbali zonse za mpandowo munali zosanjikapo manja, pamodzi ndi chifaniziro cha mkango mbali iliyonse. Mikango khumi ndi iwiri inayimirira pa makwerero asanu ndi limodziwo; mkango umodzi mbali iliyonse ya makwererowa. Mpando woterewu sunapangidwepo mu ufumu wina uliwonse. Zomwera zonse za Mfumu Solomoni zinali zagolide, ziwiya zonse za Nyumba Yaufumu ya Nkhalango ya Lebanoni zinali zagolide weniweni. Panalibe chimene chinapangidwa ndi siliva chifukwa siliva sankayesedwa kanthu pa nthawi ya Solomoni. Mfumu inali ndi sitima zapamadzi zomwe zinali pa nyanja pamodzi ndi sitima za Hiramu. Kamodzi pakapita zaka zitatu zinkabwera zitanyamula golide, siliva ndi minyanga ya njovu, anyani ndi apusi.
Mfumu Solomoni inali yopambana pa chuma ndi pa nzeru kuposa mafumu ena onse pa dziko lapansi. Anthu onse a dziko lapansi ankafunafuna kuyankhulana ndi Solomoni kuti amve nzeru zimene Mulungu anayika mu mtima mwake. Chaka ndi chaka aliyense amene amabwera ankabweretsa mphatso za siliva ndi golide, mikanjo, zida zankhondo ndi zokometsera zakudya, akavalo ndi abulu.
Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndiponso oyendetsa akavalo 12,000, zimene anazisunga mʼmizinda ya magaleta ndiponso mu Yerusalemu. Mfumu inachititsa kuti siliva akhale ngati miyala wamba mu Yerusalemu, ndipo mkungudza unali wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya mʼmbali mwa phiri. Akavalo a Solomoni ankachokera ku Igupto komanso ku Kuwe. Anthu a malonda a mfumu ankatengera akavalowo ku Kuwe. Ankagula magaleta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva okwana 600, ndipo akavalo pa mtengo wa masekeli 150. Anthu amalondawo ankagulitsa zimenezi kwa mafumu onse a Ahiti ndi Asiriya.
Akazi a Solomoni
Komatu Mfumu Solomoni anakonda akazi ambiri achilendo ndipo kuwonjezera pa mwana wamkazi wa Farao, analinso ndi akazi a mitundu iyi: Amowabu, Aamoni, Aedomu, Asidoni, ndi Ahiti. Akazi amenewa anali ochokera ku mitundu ija imene Yehova anawuza Aisraeli kuti, “Simuyenera kudzakwatirana nawo amenewa, chifukwa ndithu, amenewa adzatembenuza mitima yanu kuti mutsatire milungu yawo.” Komabe Solomoni anawakonda kwambiri akazi amenewa. Iye anali ndi akazi 700 ochokera ku mabanja achifumu ndi azikazi 300 ndipo akaziwo anamusocheretsa. Solomoni atakalamba, akazi akewo anakopa mtima wake kuti atsatire milungu ina, ndipo sanatsatire Yehova Mulungu wake ndi mtima wodzipereka, monga unalili mtima wa Davide abambo ake. Pakuti iye ankapembedza Asitoreti, mulungu wamkazi wa Asidoni, ndiponso Moleki mulungu wonyansa wa Aamoni. Kotero Solomoni anachita zoyipa pamaso pa Yehova. Sanatsatire Yehova kwathunthu monga anachitira Davide abambo ake.
Pa phiri la kummawa kwa Yerusalemu, anamanga malo opembedzerapo Kemosi, mulungu wonyansa wa Mowabu, ndiponso malo a Moleki, mulungu wonyansa wa Aamoni. Iye anamangiranso malo oterewa akazi ake onse achilendo, amene amafukiza lubani ndi kumapereka nsembe kwa milungu yawo.
Choncho Yehova anakwiyira Solomoni chifukwa mtima wake unatembenuka kuchoka kwa Yehova Mulungu wa Israeli, amene anamuonekera kawiri konse. Ngakhale kuti Yehova anamuletsa Solomoni kutsatira milungu ina, iyeyo sanamvere lamulo la Yehova. Pamenepo Yehova anati kwa Solomoni, “Popeza mtima wako ndi wotere ndipo sunasunge pangano langa ndi malamulo anga amene ndinakuwuza, ndithudi, Ine ndidzawugawa ufumuwu kuwuchotsa kwa iwe ndi kuwupereka kwa mmodzi mwa atumiki ako. Koma chifukwa cha Davide abambo ako, sindidzachita zimenezi iwe uli moyo. Ndidzawugawa mʼdzanja la mwana wako. Komabe sindidzamulanda ufumu wonse, koma ndidzamusiyira fuko limodzi chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso chifukwa cha Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha.”
Adani a Solomoni
Ndipo Yehova anamuutsira Solomoni mdani, Hadadi Mwedomu, wochokera ku banja laufumu ku Edomu. Kale pamene Davide ankachita nkhondo ndi Aedomu, Yowabu mkulu wa ankhondo, amene anapita kukakwirira Aisraeli akufa, anakantha amuna onse ku Edomu. Yowabu ndi Aisraeli onse anakhala kumeneko miyezi isanu ndi umodzi mpaka anawononga amuna onse a ku Edomu. Koma Hadadi akanali mwana anathawira ku Igupto pamodzi ndi akuluakulu ena a ku Edomu amene ankatumikira abambo ake. Iwo ananyamuka ku Midiya ndi kupita ku Parani. Ndipo anatenga amuna ena ku Paraniko, napita nawo ku Igupto, kwa Farao mfumu ya Igupto, amene anamupatsa nyumba, malo ndiponso chakudya.
Farao anamukomera mtima Hadadi ndipo anamupatsa mkazi amene anali mngʼono wake wa Mfumukazi Tahipenesi. Mngʼono wake wa Tahipenesi anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Genubati, amene analeredwa mʼnyumba yaufumu ndi Tahipenesi. Genubatiyo ankakhala limodzi ndi ana a Farao.
Ali ku Iguptoko, Hadadi anamva kuti Davide ndi Yowabu anamwalira. Pamenepo Hadadi anati kwa Farao, “Loleni ndichoke kuti ndibwerere ku dziko la kwathu.”
Farao anafunsa kuti, “Kodi ukusowa chiyani kuno kuti ufune kubwerera ku dziko la kwanu?”
Hadadi anayankha kuti, “Palibe chimene ndikusowa, koma loleni kuti ndichoke!”
Ndipo Mulungu anawutsira Solomoni mdani wina, Rezoni mwana wa Eliada, amene anali atathawa mbuye wake, Hadadezeri mfumu ya ku Zoba. Iye anasonkhanitsa anthu ndipo anali mtsogoleri wa anthu owukira pamene Davide anapha ankhondo a ku Zoba. Anthu owukirawa anapita ku Damasiko, nakakhala kumeneko ndi kuyamba kulamulira. Rezoni anali mdani wa Israeli pa masiku onse a Solomoni, kuwonjezera pa mavuto amene ankabweretsa Hadadi. Kotero Rezoni ankalamulira ku Aramu ndipo ankadana ndi Israeli.
Yeroboamu Awukira Solomoni
Yeroboamu, mwana wa Nebati anawukiranso mfumu. Iye anali mmodzi mwa akuluakulu a Solomoni wa fuko la Efereimu, wa ku Zeredi, ndipo amayi ake anali Zeruya, mkazi wamasiye.
Nkhani ya kuwukira kwa Yeroboamu inali yotere: Solomoni anamanga malo a chitetezo a Milo ndipo anakonza khoma logumuka la mzinda wa Davide, abambo ake. Tsono Yeroboamu anali munthu wamphamvu kwambiri ndipo Solomoni ataona kuti mnyamatayo amadziwa kugwira ntchito bwino, anamuyika kukhala woyangʼanira anthu a ntchito onse a nyumba ya Yosefe.
Tsiku lina Yeroboamu ali pa ulendo kuchokera ku Yerusalemu, anakumana ndi mneneri Ahiya pa msewu, ndipo Ahiyayo anali atavala mwinjiro watsopano. Awiriwo anali okha kuthengoko, ndipo Ahiya anagwira mwinjiro watsopano umene anavala ndi kuwungʼamba zidutswa 12. Tsono iye anati kwa Yeroboamu, “Tenga zidutswa khumi, pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Taona, Ine ndidzachotsa ufumu mʼdzanja la Solomoni ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. Koma chifukwa cha mtumiki wanga Davide ndiponso mzinda wa Yerusalemu, umene ndinawusankha pakati pa mafuko a Israeli, iye adzakhala ndi fuko limodzi lokha. Ndidzachita zimenezi chifukwa wandisiya Ine ndi kupembedza Asitoreti mulungu wamkazi wa Asidoni, Kemosi mulungu wa Amowabu ndiponso Moleki mulungu wa Aamoni, ndipo sanayende mʼnjira yanga, kapena kusunga mawu anga ndi malamulo anga monga anachitira Davide abambo ake.
“ ‘Koma sindidzalanda ufumu wonse mʼdzanja la Solomoni. Ine ndamuyika kukhala wolamulira masiku onse a moyo wake chifukwa cha mtumiki wanga Davide, amene ndinamusankha ndiponso amene anamvera malamulo anga ndi mawu anga. Ndidzalanda ufumu mʼdzanja la mwana wake ndipo ndidzakupatsa iwe mafuko khumi. Ndidzapereka fuko limodzi kwa mwana wake ndi cholinga choti Davide mtumiki wanga adzakhale nyale nthawi zonse pamaso panga mu Yerusalemu, mzinda umene ndinawusankha kuyikamo Dzina langa. Koma kunena za iwe, ndidzakutenga ndipo udzalamulira chilichonse chimene mtima wako ukukhumba; udzakhala mfumu ya Israeli. Ngati udzamvera zonse zimene ndidzakulamula ndi kuyenda mʼnjira yanga ndi kuchita zabwino pamaso panga, posunga malamulo anga ndi mawu anga monga anachitira Davide mtumiki wanga, Ine ndidzakhala nawe. Ndidzakupatsa ufumu umene udzakhala wokhazikika monga ndinamupatsira Davide, ndipo Ine ndidzakupatsa Israeli. Ine ndidzalanga zidzukulu za Davide chifukwa cha zimenezi, koma osati kwamuyaya.’ ”
Solomoni anafunitsitsa kupha Yeroboamu, koma Yeroboamu anathawira ku Igupto, kwa Sisaki mfumu ya Igupto ndipo anakhala kumeneko mpaka Solomoni atamwalira.
Kumwalira kwa Solomoni
Ntchito zina za Solomoni, zonse zomwe anachita komanso za nzeru zake, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya Solomoni? Solomoni analamulira Aisraeli onse mu Yerusalemu kwa zaka makumi anayi. Ndipo anagona ndi makolo ake nayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide abambo ake. Ndipo Rehobowamu mwana wake analowa ufumu mʼmalo ake.
Aisraeli Awukira Rehobowamu
Rehobowamu anapita ku Sekemu, pakuti Aisraeli onse nʼkuti atapita kumeneko kukamulonga ufumu. Yeroboamu mwana wa Nebati anamva zimenezi. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamuyo akukhala ku Igupto, pakuti atathawa Mfumu Solomoni iyeyo anakakhala ku Igupto. Tsono anthu anayitanitsa Yeroboamu, ndipo iye pamodzi ndi gulu lonse la ku Israeli anapita kwa Rehobowamu ndipo anamuwuza kuti, “Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa kwambiri, koma inu chepetsani ntchito yowawa pa ife ndipo peputsani goli lolemetsa limene anatisenzetsa. Mukatero tidzakutumikirani.”
Rehobowamu anayankha kuti, “Pitani, ndipo pakatha masiku atatu, mudzabwerenso.” Choncho anthuwo anapitadi.
Ndipo Mfumu Rehobowamu anapempha nzeru kwa akuluakulu amene ankatumikira Solomoni abambo ake pamene anali ndi moyo. Iye anawafunsa kuti, “Kodi mungandilangize zotani kuti ndiwayankhe anthu amenewa?”
Iwo anayankha kuti, “Ngati lero mudzakhala mtumiki wa anthu amenewa ndi kuwatumikira ndipo mukawayankha bwino, iwowo adzakhala atumiki anu nthawi zonse.”
Koma Rehobowamu anakana malangizo amene akuluakuluwo anamupatsa ndipo anafunsira nzeru kwa anyamata anzake amene anakulira nawo limodzi omwe ankamutumikira. Iye anawafunsa kuti, “Kodi malangizo anu ngotani? Kodi ndiwayankhe chiyani anthu amene akunena kwa ine kuti, ‘Peputsani goli limene abambo anu anatisenzetsa’?”
Anyamata anzake amene anakula nawo limodzi aja anamuyankha kuti, “Anthu amene ananena kwa iwe kuti, ‘Abambo anu anatisenzetsa goli lolemetsa, koma inu peputsani goli lathu,’ uwawuze kuti ‘Chala changa chakanise nʼchachikulu kupambana chiwuno cha abambo anga. Abambo anga ankakusenzetsani goli lolemetsa koma ine ndidzachititsa kuti likhale lolemera kwambiri. Abambo anga ankakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.’ ”
Patapita masiku atatu, Yeroboamu pamodzi ndi anthu onse anabwera kwa Rehobowamu, monga momwe inanenera mfumu kuti, “Mudzabwere pakatha masiku atatu.” Mfumuyo inawayankha anthuwo mwankhanza. Kukana malangizo amene akuluakulu anayipatsa. Anatsatira malangizo amene anyamata anzake anamupatsa ndipo anati “Abambo anga ankakusenzetsani goli lolemetsa. Ine ndidzachititsa kuti likhale lolemera kwambiri. Abambo anga ankakukwapulani ndi zikoti wamba koma ine ndidzakukwapulani ndi zinkhanira.” Choncho mfumu sinamvere pempho la anthuwo, pakuti zinthu izi zinali zochokera kwa Yehova, kukwaniritsa mawu amene Yehova anayankhula kwa Yeroboamu mwana wa Nebati kudzera mwa Ahiya wa ku Silo.
Aisraeli onse ataona kuti mfumu yakana kumva zopempha zawo, iwo anayankha mfumu kuti,
“Kodi ife tili ndi gawo lanji mwa Davide,
ndi gawo lanjinso mwa mwana wa Yese?
Inu Aisraeli, bwererani ku matenti anu!
Ziyangʼanira nyumba yako, Iwe Davide!”
Kotero Aisraeli anachoka napita ku nyumba zawo. Koma Aisraeli amene ankakhala mʼmizinda ya Yuda ankalamuliridwa ndi Rehobowamu.
Mfumu Rehobowamu anatuma Adoramu amene ankayangʼanira ntchito yathangata, koma Aisraeli onse anamugeda ndi miyala mpaka kumupha. Koma Mfumu Rehobowamu anakwera msangamsanga galeta wake nathawira ku Yerusalemu. Choncho Aisraeli akhala akuwukira nyumba ya Davide mpaka lero lino.
Aisraeli onse atamva kuti Yeroboamu wabwerera kuchokera ku Igupto, anatumiza mawu okamuyitana kuti abwere ku msonkhano ndipo anamuyika kukhala mfumu ya Aisraeli onse. Fuko la Yuda lokha ndi lomwe linkatsatira nyumba ya Davide.
Rehobowamu atafika ku Yerusalemu, anasonkhanitsa nyumba yonse ya Yuda ndi fuko la Benjamini, nasankha ankhondo okwanira 180,000, kuti akamenyane ndi nyumba ya Israeli kuti amubwezere Rehobowamu mwana wa Solomoni ufumu wake.
Koma Mulungu anayankhula ndi Semaya, munthu wa Mulungu kuti, “Nena kwa Rehobowamu mwana wa Solomoni mfumu ya Yuda, kwa nyumba yonse ya Yuda ndi Benjamini, ndiponso kwa anthu ena onse kuti, ‘Yehova akuti: Musapite kukamenyana ndi abale anu Aisraeli. Aliyense wa inu abwerere kwawo, pakuti zimenezi ndachita ndine.’ ” Choncho anthuwo anamvera mawu a Yehova ndi kubwerera kwawo, monga analamulira Yehova.
Mafano a Golide a Ana Angʼombe ku Beteli ndi ku Dani
Tsono Yeroboamu anamanga mzinda wa Sekemu mʼdziko la mapiri la Efereimu ndipo anakhala kumeneko. Kuchokera kumeneko anapita kukamanga mzinda wa Penueli.
Yeroboamu anaganiza mu mtima mwake kuti, “Ndithu, ufumuwu udzabwereranso ku nyumba ya Davide. Ngati anthuwa azipitabe kukapereka nsembe ku Nyumba ya Yehova ku Yerusalemu, adzayambanso kutsatira mbuye wawo Rehobowamu, mfumu ya Yuda. Adzandipha ndi kubwerera kwa Mfumu Rehobowamu.”
Itapempha nzeru, mfumuyo inapanga mafano awiri a ana angʼombe. Mfumuyo inati kwa anthuwo, “Mwakhala mukupita ku Yerusalemu nthawi yayitali. Iwe Israeli, nayi milungu yako imene inakutulutsa mʼdziko la Igupto.” Fano lina analiyika ku Beteli ndipo lina analiyika ku Dani. Ndipo zimenezi zinachimwitsa anthu pakuti anthu ankapita mpaka ku Dani kukapembedza fano limene linali kumeneko.
Yeroboamu anamanga Nyumba za Mulungu pa malo azipembedzo nasankha ansembe kuchokera pakati pa anthu wamba, ngakhale sanali Alevi. Iye anakhazikitsa chikondwerero pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, lofanana ndi tsiku la chikondwerero cha ku Yuda, ndipo ankapereka nsembe pa guwa. Izi ankachita ku Beteli, kupereka nsembe kwa ana angʼombe amene anapanga. Ndipo ku Beteliko anayikako ansembe pa malo achipembedzo amene anamanga. Tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chitatu, mwezi umene anawusankha yekha, anapereka nsembe pa guwa limene analimanga ku Beteli. Motero anakhazikitsa chikondwerero cha Aisraeli ndipo iye ankapita kukapereka nsembe yofukiza lubani pa guwa.
Munthu wa Mulungu Wochokera ku Yuda
Ndipo taonani, munthu wa Mulungu wochokera ku Yuda anapita ku Beteli molamulidwa ndi Yehova. Nthawi imeneyo nʼkuti Yeroboamu atayimirira pambali pa guwa akufukiza lubani. Mneneriyo anatemberera guwalo mofuwula potsata mawu a Yehova nati: “Guwa iwe, guwa iwe! Yehova akuti, ‘Taonani mʼbanja la Davide mudzabadwa mwana dzina lake Yosiya. Pa iwe, iyeyo adzaperekapo ngati nsembe, ansembe otumikira ku malo achipembedzo amene tsopano akufukiza lubani pa iwe, ndipo pa iwe adzatenthapo mafupa a anthu.’ ” Tsiku lomwelo munthu wa Mulungu uja anapereka chizindikiro ichi: “Chizindikiro chimene Yehova wanena ndi ichi: Taonani guwali lidzangʼambika pakati ndipo phulusa lili pamenepo lidzamwazika.”
Mfumu Yeroboamu atamva zimene munthu wa Mulungu ananena motemberera guwa lansembe ku Beteli, anatambasula dzanja lake ali ku guwako ndipo anati, “Mugwireni!” Koma dzanja limene anatambasula kuloza munthu wa Mulunguyo linawuma kuti gwaa, kotero kuti sanathenso kulibweza. Nthawi yomweyo guwa lija linangʼambika pakati ndipo phulusa lake linamwazika molingana ndi chizindikiro chimene munthu wa Mulungu anapereka potsata mawu a Yehova.
Pamenepo mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Undipempherere kwa Yehova Mulungu wako kuti andikomere mtima ndipo undipempherere kuti dzanja langa lichire.” Choncho munthu wa Mulungu anapempha kwa Yehova, ndipo dzanja la mfumu linachiritsidwa nʼkukhala ngati momwe linalili kale.
Mfumu inati kwa munthu wa Mulunguyo, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya, ndipo ndidzakupatsa mphatso.”
Koma munthu wa Mulunguyo anayankha mfumu kuti, “Ngakhale mutandipatsa theka la chuma chanu, sindingapite nanu, kapena kudya chakudya, kapenanso kumwa madzi kuno. Pakuti Yehova anandilamula kuti, ‘Usakadye chakudya kapena kumwa madzi kapena kubwerera podzera njira imene unayendamo kale.’ ” Choncho munthu wa Mulunguyo anadzera njira ina ndipo sanatsate njira imene anayendamo pobwera ku Beteliko.
Tsono ku Beteli kunkakhala mneneri wina wokalamba. Mmodzi mwa ana ake anamufotokozera zonse zomwe munthu wa Mulungu anachita kumeneko tsiku limenelo. Anawuzanso abambo ake zimene ananena kwa mfumu. Abambo awo aja anawafunsa kuti, “Kodi wadzera njira iti?” Ana akewo anamufotokozera njira imene munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo anadzera. Ndipo abambo aja anati kwa ana akewo, “Mangireni chishalo pa bulu.” Anawo atamangirira chishalo pa bulu, nkhalambayo inakwera buluyo ndipo inalondola munthu wa Mulunguyo. Inamupeza atakhala pansi pa mtengo wa thundu ndipo inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe munthu wa Mulungu amene anabwera kuchokera ku Yuda?”
Munthuyo anayankha kuti, “Inde, ndineyo.”
Choncho mneneri wokalambayo anati kwa iye, “Tiye kwathu kuti ukadye chakudya.”
Munthu wa Mulungu uja anati, “Sindingabwerere nanu kapena kudya chakudya kapenanso kumwa madzi kuno. Pakuti ndawuzidwa ndi Yehova kuti, ‘Usadye chakudya kapena kumwa madzi kumeneko kapenanso kubwerera poyenda njira imene unayendamo popita.’ ”
Mneneri wokalambayo anayankha kuti, “Inenso ndine mneneri ngati iwe. Ndipo mngelo wa Yehova anayankhula nane mawu a Yehova kuti, ‘Kamubweze abwere ku nyumba yako kuti akadye chakudya ndi kumwa madzi.’ ” Koma anamunamiza. Choncho munthu wa Mulungu uja anabwerera naye ndipo anakadya ndi kumwa madzi mʼnyumba mwake.
Ali pa tebulo, Yehova anayankhula ndi mneneri wokalambayo amene anamubweza munthu wa Mulunguyo. Iye anafuwulira munthu wa Mulungu wochokera ku Yudayo kuti, “Yehova akuti, ‘Iwe wanyoza mawu a Yehova ndipo sunasunge lamulo limene Yehova Mulungu wako anakupatsa. Iwe wabwerera ndi kudya chakudya ndiponso kumwa madzi ku malo amene Iye anakuwuza kuti usadye chakudya kapena kumwa madzi. Choncho mtembo wako sadzawuyika mʼmanda a makolo ako.’ ”
Munthu wa Mulungu atatha kudya ndi kumwa, mneneri amene anamubweza uja anamangirira chishalo pa bulu wa munthu wa Mulunguyo. Akupita, anakumana ndi mkango pa msewu ndipo unamupha, mtembo wake unagwera pansi pa msewu, bulu uja anayima pambali pake ndipo mkango unayima pafupi ndi mtembowo. Ndipo taonani, anthu ena amene ankapita mu msewumo anaona mtembowo uli pansi potero, mkango utayima pa mbali pa mtembo uja ndipo anapita nakafotokozera anthu mu mzinda umene mumakhala mneneri wokalamba uja.
Mneneri amene anamubweza mnzake ku njira uja atamva zimenezi, anati, “Ameneyo ndi munthu wa Mulungu amene wanyoza mawu a Yehova. Yehova wamupereka kwa mkango umene wamukhadzula ndi kumupha, monga momwe Yehova anamuchenjezera.”
Mneneri wokalambayo anati kwa ana ake, “Mundimangire chishalo pa bulu,” ndipo anaterodi. Ndipo anapita, nakapezadi mtembo utagwera pansi mu msewu, bulu pamodzi ndi mkango atayima pambali pake. Koma mkangowo sunadye mtembowo kapena kukhadzula buluyo. Choncho mneneri wokalambayo anatenga mtembo wa munthu wa Mulunguyo, nawuyika pa bulu, ndipo anabwera nawo ku mzinda kuti alire maliro ndi kuyika mtembowo mʼmanda. Tsono anayika mtembowo mʼmanda amene mneneri wokalamba uja anadzikonzera, ndipo anamulira pomanena kuti, “Mʼbale wanga ine! Mʼbale wanga ine!”
Atamuyika mʼmanda, iye anati kwa ana ake, “Ine ndikafa, mudzandiyike mʼmanda amene munthu wa Mulungu wayikidwa. Mudzayike mafupa anga pambali pa mafupa ake. Pakuti uthenga umene Yehova anamuyankhulitsa, wotsutsana ndi guwa lansembe la ku Beteli ndi nyumba zonse za chipembedzo za mʼmizinda ya ku Samariya, zidzachitika ndithu.”
Ngakhale izi zinachitika, Yeroboamu sanasiye njira zake zoyipa, koma anasankhanso anthu wamba kukhala ansembe pa malo ake achipembedzo. Aliyense amene ankafuna kukhala wansembe iye anamupatula kukhala wansembe. Limeneli ndiye linali tchimo la nyumba ya Yeroboamu limene linabweretsa kugwa kwake ndiponso chiwonongeko mʼdzikomo.
Ahiya Anenera za Kugwa kwa Yeroboamu
Pa nthawi imeneyo Abiya mwana wa Yeroboamu anayamba kudwala, ndipo Yeroboamu anati kwa mkazi wake, “Nyamuka ndipo udzibise kuti usadziwike kuti ndiwe mkazi wa Yeroboamu, ndipo upite ku Silo. Kumeneko kuli mneneri Ahiya amene anandiwuza kuti ndidzakhala mfumu ya anthu awa. Utenge buledi khumi, makeke ndiponso botolo la uchi ndipo upite kwa mneneriyo. Iye adzakuwuza zimene zidzamuchitikire mwanayu.” Choncho mkazi wa Yeroboamu anadzibisa ndipo anapita ku nyumba ya Ahiya ku Silo.
Tsono Ahiya sankatha kupenya bwino. Ankangoona kuti mbuu chifukwa cha ukalamba. Koma Yehova nʼkuti atamuwuza Ahiya kuti, “Taona, mkazi wa Yeroboamu akubwera kudzafunsa iwe za mwana wake pakuti akudwala, ndiye udzamuyankhe zakutizakuti mkaziyo. Iye akafika, adzadzibisa.”
Tsono Ahiya atamva mgugu wa mapazi ake pa khomo, anati, “Lowa, iwe mkazi wa Yeroboamu. Bwanji ukudzibisa? Ine ndatumidwa kuti ndikuwuze nkhani yoyipa. Pita, kamuwuze Yeroboamu kuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ine ndinakukweza pakati pa anthu ndipo ndinakuyika kukhala mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli. Ndinachotsa ufumu ku nyumba ya Davide ndi kuwupereka kwa iwe, koma iwe sunafanane ndi mtumiki wanga Davide, amene ankasunga malamulo anga ndi kunditsata Ine ndi mtima wake wonse, kuchita zolungama zokhazokha pamaso panga. Ndipo iwe wachita zoyipa kupambana onse amene analipo kale. Wadzipangira milungu ina, mafano a zitsulo. Iweyo wandikwiyitsa ndipo wandiwukira.
“ ‘Choncho taona, ndidzabweretsa masautso pa nyumba ya Yeroboamu. Ndipo ndidzawononga munthu wamwamuna aliyense wa pa banja lako, kapolo pamodzi ndi mfulu yemwe mʼdziko la Israeli. Ndidzatentha nyumba ya Yeroboamu monga mmene munthu amatenthera ndowe mpaka yonse kutheratu. Agalu adzadya aliyense wa banja la Yeroboamu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame zamlengalenga zidzadya iwo amene adzafere ku thengo, pakuti Yehova watero!’
“Ndipo iwe nyamuka, bwerera ku nyumba kwako. Phazi lako likadzangoponda mu mzindamo, mwanayo adzamwalira. Aisraeli onse adzalira maliro ake ndi kumuyika mʼmanda. Ndi yekhayo wa banja la Yeroboamu amene adzayikidwe mʼmanda, pakuti ndi mwa iye yekha mmene Yehova Mulungu wa Israeli wapezamo kanthu kabwino.
“Koma Yehova adzadzisankhira yekha mfumu yolamulira Israeli imene idzawononga banja la Yeroboamu. Tsiku lake ndi lero! Ndati chiyani? Inde, ndi lero lomwe lino. Ndipo Yehova adzakantha Israeli, kotero kuti adzakhala ngati bango logwedera pa madzi. Iye adzazula Israeli mʼdziko labwino limene analipereka kwa makolo ake ndi kuwamwazira kutsidya kwa mtsinje wa Yufurate, chifukwa anakwiyitsa Yehova pamene anapanga mafano a Asera. Ndipo Iye sadzasamalanso Israeli chifukwa cha machimo amene anachita Yeroboamu ndi kuchimwitsa nawo Israeli.”
Tsono mkazi wa Yeroboamu anayimirira nachoka kupita ku Tiriza. Atangoponda pa khonde la nyumba yake, mwana uja anamwalira. Aisraeli anamuyika mʼmanda, ndipo onse analira maliro ake, monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa mtumiki wake, mneneri Ahiya.
Ntchito zina pa nthawi ya ulamuliro wa Yeroboamu, nkhondo zake ndi mmene ankalamulirira zinalembedwa mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli. Iye analamulira zaka 22 ndipo anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Nadabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Rehobowamu Mfumu ya Yuda
Rehobowamu mwana wa Solomoni anali mfumu ya ku Yuda. Iye analowa ufumu ali ndi zaka 41, ndipo analamulira zaka 17 ku Yerusalemu, mzinda umene Yehova anawusankha pakati pa mafuko a Israeli kuti ayikemo Dzina lake. Amayi ake anali Naama, wa ku Amoni.
Anthu a ku Yuda anachita zoyipa pamaso pa Yehova kupambana mmene anachitira makolo awo ndipo Yehova anawakwiyira. Iwonso anadzipangira malo opembedzerapo mafano pa chitunda chilichonse ndi kuyimika miyala ya chipembedzo ndi mitengo ya Asera pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri. Mʼdzikomo munalinso amuna ochita zachiwerewere mwa chipembedzo. Anthu ankachita zonyansa zonse za anthu a mitundu ina imene Yehova anayipirikitsa asanafike Aisraeli.
Chaka chachisanu cha ufumu wa Rehobowamu, Sisaki, mfumu ya Igupto, anadzathira nkhondo Yerusalemu. Ananyamula chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso chuma cha ku nyumba ya mfumu. Anatenga chilichonse, ngakhalenso zishango zonse zagolide zimene Solomoni anapanga. Ndipo Mfumu Rehobowamu anapanga zishango zamkuwa mʼmalo mwake, nazipereka mʼmanja mwa olamulira alonda a pa khomo pa nyumba ya mfumu. Nthawi zonse mfumu ikamapita ku Nyumba ya Yehova, alonda ankanyamula zishangozo, kenaka ankazisunga mʼchipinda cha alonda.
Tsono ntchito zina za Rehobowamu ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo zosalekeza pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. Ndipo Rehobowamu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Amayi ake anali Naama wa ku Amoni. Ndipo Abiya analowa ufumu mʼmalo mwa abambo ake.
Abiya Mfumu ya Yuda
Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Yeroboamu mwana wa Nebati, Abiya anakhala mfumu ya Yuda, ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka zitatu. Amayi ake anali Maaka, mwana wa Abisalomu.
Abiya anachita zoyipa zonse zimene abambo ake anazichita. Sanali wangwiro pamaso pa Yehova Mulungu wake, monga linachitira kholo lake Davide. Komabe chifukwa cha Davide, Yehova Mulungu wake anamupatsa nyale mu Yerusalemu pomupatsa mwana wolowa mʼmalo mwake ndi kumukhazikitsa kukhala wamphamvu mu Yerusalemu; pakuti Davide anachita zolungama pamaso pa Yehova ndipo sanalephere kusunga chilichonse chimene Yehova anamulamula masiku onse a moyo wake kupatula nkhani ija ya Uriya Mhiti.
Panali nkhondo pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu masiku onse a moyo wa Abiya. Tsono ntchito zina za Abiya, ndi zina zonse anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Panali nkhondo pakati pa Abiya ndi Yeroboamu. Ndipo Abiya anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu Mzinda wa Davide. Ndipo Asa, mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Asa Mfumu ya Yuda
Mʼchaka cha makumi awiri cha Yeroboamu mfumu ya Israeli, Asa anakhala mfumu ya Yuda, ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 41. Agogo ake akazi anali Maaka mwana wa Abisalomu.
Asa anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zadama pochita chipembedzo chawo ndiponso anachotsa mafano onse amene makolo ake anawapanga. Iye anachotsanso gogo wake Maaka pa udindo wake wa amayi a mfumu, chifukwa choti anapanga fano lonyansa la Asera. Asa anagwetsa fanolo nakalitentha ku Chigwa cha Kidroni. Ngakhale sanachotse malo opembedzerapo mafano, mtima wa Asa unali wodzipereka kwathunthu kwa Yehova masiku onse a moyo wake. Asa anabweretsa ku Nyumba ya Yehova zinthu zimene abambo ake anazipereka, ndiponso zinthu zimene iye mwini anazipereka: zagolide, siliva ndi ziwiya zotengera.
Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli nthawi yonse ya ulamuliro wawo. Baasa mfumu ya Israeli anapita kukathira nkhondo dziko la Yuda, ndipo anamangira linga mzinda wa Rama kuletsa kuti wina aliyense asatuluke kapena kulowa mʼdziko la Asa, mfumu ya Yuda.
Tsono Asa anatenga siliva yense pamodzi ndi golide zimene zinatsala ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Yehova ndiponso ku nyumba yake yaufumu. Anazipereka kwa atumiki ake, nawatuma kupita nazo kwa Beni-Hadadi mwana wa Tabirimoni, mwana wa Heziyoni, mfumu ya Aramu, amene ankakhala ku Damasiko ndipo anakamuwuza kuti, “Tiyeni tigwirizane inu ndi ine, monga panali mgwirizano pakati pa abambo anu ndi abambo anga. Onani, ndikukutumizirani mphatso za siliva ndi golide. Tsopano kathetseni mgwirizano wanu ndi Baasa mfumu ya Israeli kuti andisiye.”
Choncho Beni-Hadadi anamvera zimene ananena mfumu Asa ndipo anatumiza olamulira magulu ake ankhondo ku mizinda ya Israeli. Ndipo iye anagonjetsa Iyoni, Dani, Abeli-Beti-Maaka ndi dera lonse la Kinereti kuphatikiza dziko lonse la Nafutali. Baasa atamva zimenezi, anasiya kumangira linga Rama ndipo anakakhala ku Tiriza. Pamenepo Mfumu Asa analamula anthu onse a ku Yuda osasiya ndi mmodzi yemwe, ndipo anachotsa ku Rama miyala ndi matabwa amene Baasa ankamangira kumeneko. Zipangizo zimenezi Mfumu Asa inamangira linga la Geba ku Benjamini ndi la ku Mizipa.
Tsono ntchito zina za Asa, za mphamvu zake ndi mizinda imene anayimanga ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Yuda? Koma pa nthawi ya ukalamba wake anadwala nthenda ya mapazi. Ndipo Asa anamwalira nayikidwa mʼmanda momwe anayikidwa makolo ake mu mzinda wa Davide kholo lake. Ndipo Yehosafati mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Nadabu Mfumu ya Israeli
Nadabu, mwana wa Yeroboamu anakhala mfumu ya Israeli mʼchaka chachiwiri cha Asa mfumu ya Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. Nadabu anachita zoyipa pamaso pa Yehova, anayenda mʼnjira za abambo ake ndi mu uchimo womwe anachimwitsa nawo Israeli.
Baasa mwana wa Ahiya, wa banja la Isakara anakonzera Nadabuyo chiwembu, ndipo anamukantha ku Gibetoni, mzinda wa Afilisti, pamene Nadabu ndi anthu onse a ku Israeli anali atawuzungulira. Baasa anapha Nadabu mʼchaka chachitatu cha Asa, mfumu ya ku Yuda ndipo analowa ufumu mʼmalo mwake.
Iye atangoyamba kulamulira, anapha anthu onse a banja la Yeroboamu. Sanasiye ndi mmodzi yemwe wamoyo pa banjapo, koma anawononga anthu onse, molingana ndi mawu a Yehova amene anayankhula mwa mtumiki wake Ahiya wa ku Silo chifukwa cha machimo amene Yeroboamu anachita, ndiponso kuchimwitsa anthu a ku Israeli, naputa mkwiyo wa Yehova Mulungu wa Israeli.
Tsono ntchito za Nadabu ndi zina zonse zimene anazichita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Panali nkhondo pakati pa Asa ndi Baasa mfumu ya Israeli pa nthawi yonse ya ulamuliro wawo.
Baasa Mfumu ya Israeli
Chaka chachitatu cha Asa mfumu ya Yuda, Baasa mwana wa Ahiya anakhala mfumu ya Aisraeli onse ku Tiriza, ndipo analamulira zaka 24. Anachita zoyipa pamaso pa Yehova, nayenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchita tchimo lake limene linachimwitsa anthu a ku Israeli.
Ndipo Yehova anayankhula kudzera mwa Yehu mwana wa Hanani, mawu odzudzula Baasa kuti, “Ine ndinakukuza kuchokera pa fumbi ndipo ndinakupanga kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisraeli, koma iwe wakhala ukuyenda mʼnjira za Yeroboamu ndi kuchimwitsa anthu anga Aisraeli naputa mkwiyo wanga chifukwa cha machimo awo. Taonani, Ine ndatsala pangʼono kuwononga Baasa pamodzi ndi nyumba yake, ndipo ndidzachitira nyumba yake zimene ndinachita pa nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati. Agalu adzadya aliyense wa banja la Baasa amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya iwo amene adzafere kuthengo.”
Tsono ntchito zina za Baasa ndi zamphamvu zake zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Baasa anamwalira nayikidwa mʼmanda amene anayikidwa makolo ake ku Tiriza. Ndipo Ela mwana wake anakhala mfumu mʼmalo mwake.
Komatu Yehova anayankhula kwa Baasa pamodzi ndi banja lake lonse kudzera mwa mneneri Yehu mwana wa Hanani, chifukwa cha zoyipa zonse zimene iye anachita pamaso pa Yehova, kukwiyitsa Yehovayo nakhala ngati nyumba ya Yeroboamu ndiponso chifukwa anawonongeratu banja la Yeroboamu.
Ela Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 26 cha ufumu wa Asa mfumu ya Yuda, Ela mwana wa Baasa anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira ku Tiriza zaka ziwiri.
Zimuri, mmodzi mwa akuluakulu ake, amene ankalamulira theka la magaleta ake, anamuchitira chiwembu. Nthawi imeneyi Ela anali ku Tiriza, akumwa koledzera nako mʼnyumba ya Ariza, munthu amene ankayangʼanira nyumba yaufumu ku Tiriza. Zimuri anadzalowa, namukantha ndi kumupha mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda. Ndipo Zimuriyo anakhala mfumu mʼmalo mwake.
Zimuri atangoyamba kulamulira, anapha banja lonse la Baasa. Sanasiyepo munthu wamwamuna ndi mmodzi yemwe, wachibale kapena bwenzi lake. Choncho Zimuri anawononga banja lonse la Baasa, molingana ndi mawu amene Yehova anayankhula motsutsa Baasa kudzera mwa mneneri Yehu, chifukwa cha machimo onse amene Baasa ndi mwana wake Ela anachita nachimwitsa Israeli, anakwiyitsa Yehova, Mulungu wa Israeli ndi mafano awo osapindulitsa.
Tsono ntchito zina za Ela ndi zina zonse zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
Zimuri Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 27 cha Asa mfumu ya Yuda, Zimuri analamulira ku Tiriza masiku asanu ndi awiri. Gulu la ankhondo linali litamanga misasa pafupi ndi Gibetoni, mzinda wa Afilisti. Ankhondo amene anali ku misasa atamva kuti Zimuri wachita chiwembu ndi kupha mfumu, tsiku lomwelo ku misasako anasankha Omuri, mkulu wa ankhondo kukhala mfumu ya Israeli. Tsono Omuri ndi Aisraeli onse amene anali naye anachoka ku Gibetoni ndi kukazinga Mzinda wa Tiriza. Zimuri ataona kuti mzinda walandidwa, anathawira ku nsanja ya nyumba ya mfumu ndipo anatentha nyumbayo iye ali momwemo. Kotero iyeyo anafa, chifukwa cha machimo amene iye anachita, kuchita zoyipa pamaso pa Yehova ndi kuyenda mʼnjira za Yeroboamu, nachimwitsa nazo Aisraeli.
Tsono ntchito zina za Zimuri ndi chiwembu chake chimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli?
Omuri Mfumu ya Israeli
Pambuyo pake Aisraeli anagawikana pakati: theka linatsatira Tibini mwana wa Ginati kuti limulonge ufumu, ndipo theka lina linatsatira Omuri. Koma anthu otsatira Omuri anali amphamvu kupambana amene ankatsatira Tibini mwana wa Ginati. Choncho Tibini anafa ndipo Omuri anakhala mfumu.
Mʼchaka cha 31 cha Asa mfumu ya Yuda, Omuri anakhala mfumu ya Israeli, ndipo analamulira zaka 12 ndi miyezi isanu ndi umodzi ku Tiriza. Iye anagula phiri la Samariya kwa Semeri pa mtengo wa ndalama 6,000 za siliva ndipo pa phiripo anamangapo mzinda, nawutcha Samariya, potsata dzina la Semeri, dzina la mwini wakale wa phirilo.
Koma Omuri anachita zoyipa pamaso pa Yehova ndipo anachimwa kuposa mafumu ena onse amene analipo iye asanakhale mfumu. Pakuti iye anayenda mʼnjira zonse za Yeroboamu mwana wa Nebati, ndipo tchimo lake anachimwitsa nalo Aisraeli, nakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli ndi mafano awo opandapake.
Tsono ntchito zina za Omuri ndi zamphamvu zimene anachita, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a Israeli? Choncho Omuri anamwalira nayikidwa mʼmanda amene anayikidwa makolo ake ku Samariya. Ndipo Ahabu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ahabu Akhala Mfumu ya Israeli
Mʼchaka cha 38 cha ufumu wa Asa, mfumu ya Yuda, Ahabu mwana wa Omuri anakhala mfumu ya Israeli nalamulira Israeli ku Samariya zaka 22. Ahabu mwana wa Omuri anachita zoyipa zambiri pamaso pa Yehova kupambana mafumu onse akale. Iye sanachiyese ngati chinthu chochepa chabe kuchita machimo a Yeroboamu mwana wa Nebati, koma anakwatiranso Yezebeli, mwana wa Etibaala mfumu ya Asidoni, nayamba kutumikira Baala ndi kumupembedza. Iye anapangira Baala guwa lansembe mʼnyumba ya Baala imene anamanga ku Samariya. Ahabu anapanganso fano la Asera ndi kukwiyitsa kwambiri Yehova Mulungu wa Israeli, kupambana mafumu onse a Israeli amene analipo iye asanakhale mfumu.
Pa nthawi ya Ahabu, Hiyeli wa ku Beteli anamanganso mzinda wa Yeriko. Pa nthawi yomanga maziko ake, mwana wake woyamba wa mwamuna, Abiramu anamwalira, ndipo pa nthawi yomanga zipata zake, mwana wa mngʼono wa mwamuna Segubu, anamwaliranso. Izi zinachitika monga momwe Yehova ananenera kudzera mwa Yoswa mwana wa Nuni.
Makwangwala Adyetsa Eliya
Ndipo mneneri Eliya wa ku Tisibe ku Giliyadi, anati kwa Ahabu, “Pali Yehova wamoyo, Mulungu wa Israeli, amene ndimamutumikira, sipadzakhala mame kapena mvula zaka zikubwerazi, pokhapokha ine nditanena.”
Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, “Choka kuno, upite kummawa, ukabisale mʼmbali mwa mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani. Uzikamwa mu mtsinjemo, ndipo ndalamula makwangwala kuti azikakudyetsa kumeneko.”
Choncho Eliya anachita zomwe Yehova anamuwuza. Anapita ku mtsinje wa Keriti, pafupi ndi Yorodani, nakakhala kumeneko. Makwangwala ankabweretsera buledi ndi nyama mmawa ndi madzulo, ndipo ankamwa mu mtsinjemo.
Mayi Wamasiye wa ku Zarefati
Patapita masiku, mtsinjewo unaphwa chifukwa mvula sinagwe mʼdzikomo. Yehova anayankhula naye kuti, “Nyamuka tsopano, pita ku Zarefati ku Sidoni ndipo ukakhale kumeneko. Ndalamula mkazi wamasiye wa kumeneko kuti azikakudyetsa.” Choncho iye ananyamuka napita ku Zarefati. Atafika pa chipata cha mzindawo, taonani mkazi wamasiye amatola nkhuni. Anamuyitana ndi kumuwuza kuti, “Patseni madzi pangʼono mʼchikho kuti ndimwe.” Mayi wamasiye uja ankapita kukatunga madzi, Eliya anamuyitananso namuwuza kuti, “Chonde munditengerekonso buledi.”
Iye anayankha kuti “Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, ine ndilibe chakudya china chilichonse, koma kaufa pangʼono mʼmbiya ndi mafuta pangʼono mʼbotolo. Ine ndikutola tinkhuni tochepa kuti ndipite nato ku nyumba ndi kukaphika chakudya changa ndi cha mwana wanga, kuti tikadye kenaka tife.”
Eliya anati kwa iye, “Musachite mantha. Pitani mukachite monga mwaneneramo. Koma poyamba mundipangire kachakudya pangʼono kuchokera pa ufa umene muli nawo ndi kubwera nako kwa ine, ndipo kenaka mukaphike choti mudye inuyo ndi mwana wanuyo. Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ufa umene uli mʼmbiyamo sudzatha ndipo mafuta amene ali mʼbotolomo sadzathanso mpaka tsiku limene Yehova adzagwetse mvula pa dziko lapansi.’ ”
Mayi wamasiyeyo anapita nakachita zimene Eliya anamuwuza. Choncho panali chakudya cha Eliya, mayiyo pamodzi ndi banja lake lonse chimene anadya masiku ambiri. Pakuti ufa umene unali mʼmbiya sunathe ndiponso mafuta amene anali mʼbotolo sanathe, monga momwe ananenera Yehova kudzera mwa Eliya.
Tsiku lina mwana wake wa mkazi wamasiye uja, mwini nyumbayo, anadwala. Matenda ananka nakulirakulirabe, ndipo kenaka analeka kupuma. Mayiyo anati kwa Eliya, “Kodi ndakulakwirani chiyani, inu munthu wa Mulungu? Kodi munabwera kuno kudzandikumbutsa tchimo langa ndi kudzandiphera mwana wanga?”
Eliya anayankha kuti, “Patseni mwana wanuyo.” Iye anatenga mwanayo mʼmanja mwa mayiyo napita naye mʼchipinda chapamwamba, kumene Eliyayo amagona, namugoneka pa bedi lake. Kenaka Eliya anafuwula kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wanga, kodi mwabweretsanso choyipa chotere pa mkazi wamasiye amene ine ndikukhala naye, pakuchititsa kuti mwana wake afe?” Pamenepo Eliya anakumbatira mwanayo katatu ndi kufuwula kwa Yehova kuti, “Inu Yehova Mulungu wanga, mubwezereni mwanayu moyo wake!”
Yehova anamva kufuwula kwa Eliya, ndipo moyo wa mwanayo unabwerera mwa iye ndipo anatsitsimuka. Eliya ananyamula mwanayo natsika naye kuchoka mʼchipinda chapamwamba chija nalowa naye mʼnyumba. Anamupereka kwa amayi ake ndipo anati, “Taonani, mwana wanu ali ndi moyo!”
Pamenepo mayiyo anati kwa Eliya, “Tsopano ndadziwa kuti ndinu munthu wa Mulungu ndipo mawu a Yehova amene mumayankhula ndi owona.”
Eliya ndi Obadiya
Patapita masiku ambiri, mʼchaka chachitatu cha chilala, Yehova anayankhula ndi Eliya kuti, “Pita ukadzionetse kwa Ahabu ndipo ndidzagwetsa mvula pa dziko lapansi.” Choncho Eliya anapita kukadzionetsa kwa Ahabu.
Tsono nthawi imeneyi njala inakula kwambiri mu Samariya, ndipo Ahabu anayitana Obadiya amene ankayangʼanira nyumba yake yaufumu. (Obadiya ankaopa Yehova kwambiri. Pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova, Obadiya anatenga aneneri 100 ndi kuwabisa mʼmapanga awiri, phanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ankawapatsa chakudya ndi madzi). Ahabu anawuza Obadiya kuti, “Pita mʼdziko kulikonse kumene kuli zitsime za madzi ndi ku zigwa zonse. Mwina mwake tingapeze udzu oti nʼkumadyetsa akavalo ndi abulu kuti akhale ndi moyo, kuti tisaphe chiweto chilichonse.” Choncho anagawana dziko loti apiteko, Ahabu anapita mbali ina, Obadiya nʼkupita ina.
Obadiya akuyenda mʼnjira anakumana ndi Eliya. Ndipo taonani, Obadiya anamuzindikira Eliyayo, naweramira pansi ndipo anati, “Kodi ndinu, mbuye wanga Eliya?”
Eliya anayankha kuti, “Inde. Pita kawuze mbuye wako kuti, ‘Eliya wabwera.’ ”
Obadiya anafunsa kuti, “Kodi ndalakwa chiyani kuti inu mupereke mtumiki wanu kwa Ahabu kuti akaphedwe? Pali Yehova Mulungu wanu wamoyo, kulibe mtundu wa anthu kapena ufumu uliwonse kumene mbuye wanga sanatumeko anthu okakufunafunani. Ndipo pamene mtundu wa anthu kapena ufumu unena kuti kuno kulibe, Ahabu ankawalumbiritsa kuti atsimikizedi kuti inuyo kulibe kumeneko. Koma tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ Ine sindikudziwa kumene Mzimu wa Yehova udzakupititsani ine ndikachoka. Ngati ndipita kukamuwuza Ahabu ndipo iye wosadzakupezani, adzandipha. Komatu ine mtumiki wanu ndakhala ndi kupembedza Yehova kuyambira ubwana wanga. Mbuye wanga, kodi simunamve zimene ndinachita pamene Yezebeli ankapha aneneri a Yehova? Ine ndinabisa aneneri 100 a Yehova mʼmapanga awiri, mʼphanga lililonse aneneri makumi asanu, ndipo ndinkawapatsa chakudya ndi madzi akumwa. Ndiye inu tsopano mukundiwuza kuti ndipite kwa mbuye wanga ndi kukanena kuti, ‘Eliya wabwera.’ Iyeyo adzandipha ndithu!”
Eliya anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse wamoyo, amene ndimamutumikira, ine lero ndidzaonekera ndithu pamaso pa Ahabu.”
Eliya pa Phiri la Karimeli
Choncho Obadiya anapita kukakumana ndi Ahabu, namuwuza, ndipo Ahabu anapita kukakumana ndi Eliya. Pamene Ahabu anaona Eliya, anati kwa iye, “Kodi ndiwedi, munthu wovutitsa Israeli uja?”
Eliya anayankha kuti, “Ine sindinavutitse Israeli, koma ndinuyo ndi banja lanu. Mwasiya malamulo a Yehova ndipo mwatsatira Abaala. Tsopano sonkhanitsani anthu a mʼdziko lonse la Israeli kuti akumane nane pa Phiri la Karimeli. Ndipo mubwere nawo aneneri a Baala 450 ndi aneneri a fano la Asera 400, amene amadya pa tebulo la Yezebeli.”
Choncho Ahabu anatumiza mawu mʼdziko lonse la Israeli, ndipo anasonkhanitsa aneneri a Baala ku Phiri la Karimeli. Eliya anapita patsogolo pa anthuwo ndipo anati, “Kodi mudzakhala anthu a mitima iwiri mpaka liti? Ngati Yehova ndi Mulungu, mutsateni; koma ngati Baala ndi Mulungu, mutsateni.”
Koma anthu aja sanayankhe.
Pamenepo Eliya ananena kwa iwo kuti, “Ine ndilipo ndekha mneneri wa Yehova, koma Baala ali ndi aneneri 450. Tibweretsereni ngʼombe zazimuna ziwiri. Iwo asankhepo okha ngʼombe imodzi, ndipo ayidule nthulinthuli ndi kuziyika pa nkhuni nthulizo, koma osakolezapo moto. Ndipo ine ndidzadula nthulinthuli ngʼombe inayo ndi kuyika pa nkhuni koma sindikolezapo moto. Kenaka inu muyitane dzina la mulungu wanu, ndipo ine ndidzayitana dzina la Yehova. Mulungu amene ati ayankhe potumiza moto, iyeyo ndiye Mulungu.”
Pamenepo anthu onse anati, “Izi mwanena zamveka bwino.”
Eliya anawuza aneneri a Baala kuti, “Yambani ndinu. Sankhani ngʼombe yayimuna imodzi, muyikonze, popeza mulipo ambiri. Muyitane dzina la mulungu wanu, koma musakoleze moto.” Choncho iwo anatenga ngʼombe yayimunayo imene anawapatsa, nayikonza.
Kenaka anayitana dzina la Baala kuyambira mmawa mpaka masana. Iwo anafuwula kuti, “Inu Baala, tiyankheni ife.” Koma panalibe yankho; palibe amene anayankha. Ndipo anavinavina mozungulira guwa lansembe limene anapanga.
Nthawi yamasana Eliya anayamba kuwanyogodola ndipo anati, “Fuwulani kwambiri. Ndithudi, iye ndi mulungu! Mwinatu akulingalira kwambiri, kapena watanganidwa, kapena ali paulendo. Mwina wagona ndipo nʼkofunika kuti adzutsidwe.” Choncho iwo anafuwula kwambiri ndi kudzichekacheka ndi malupanga ndi mikondo, potsata miyambo yawo, mpaka kutuluka magazi. Nthawi yamasana inadutsa, ndipo anapitiriza kunenera mwakhama mpaka nthawi yopereka nsembe ya madzulo. Koma panalibe yankho. Palibe amene anayankha, kapena kulabadira zimenezo.
Pamenepo Eliya anati kwa anthu onse, “Senderani pafupi ndi ine.” Ndipo anthu onsewo anasendera pafupi ndi iye, ndipo iye anakonza guwa lansembe la Yehova limene linali litawonongeka. Eliya anatenga miyala 12, mwala uliwonse kuyimira fuko lililonse la Yakobo, amene Yehova anamuwuza kuti, “Dzina lako lidzakhala Israeli.” Ndi miyala imeneyo anamanga guwa mʼdzina la Yehova, ndipo anakumba ngalande yayikulu yolowa malita 15 a madzi kuzungulira guwalo. Anayika nkhuni zija mʼmalo mwake nadula nthulinthuli ngʼombe yayimuna ija ndi kuyika nthulizo pa nkhunipo. Pamenepo Eliya anati, “Dzazani mitsuko inayi ndi madzi ndipo muwathire pa nyama ya nsembeyo ndi nkhunizo.”
Eliya anati, “Thiraninso kachiwiri.” Anthu aja anathiranso madziwo kachiwiri.
Iye analamula kuti, “Thiraninso kachitatu.” Ndipo iwo anathiranso kachitatu. Madziwo anayenderera pansi kuzungulira guwa lansembe, nadzaza ngalande yonse.
Pa nthawi yopereka nsembe, mneneri Eliya anasendera pafupi ndi guwa lansembe, napemphera kuti, “Inu Yehova, Mulungu wa Abrahamu, Isake ndi Yakobo, lero zidziwike kuti ndinu Mulungu mu Israeli ndipo kuti ine ndine mtumiki wanu, kuti ine ndachita zonsezi chifukwa mwalamula ndinu. Ndiyankheni, Inu Yehova, ndiyankheni, kuti anthu awa adziwe Inu Yehova, kuti ndinu Mulungu, ndipo kuti mutembenuziranso mitima yawo kwa Inu.”
Pamenepo moto wa Yehova unagwa, nunyeketsa nsembe yopserezayo, nkhuni, miyala ndi dothi lomwe. Unawumitsanso madzi amene anali mʼngalande.
Anthu onse ataona zimenezi, anaweramitsa nkhope zawo pansi, nafuwula kuti, “Yehova ndiye Mulungu! Yehova ndiye Mulungu!”
Pamenepo Eliya analamula anthuwo kuti, “Gwirani aneneri a Baala. Musalole kuti wina aliyense athawe!” Anagwira onsewo ndipo Eliya anabwera nawo ku Chigwa cha Kisoni, nawapha kumeneko.
Ndipo Eliya anati kwa Ahabu, “Pitani, kadyeni ndi kumwa, pakuti kukumveka mkokomo wa mvula.” Choncho Ahabu anapita kukadya ndi kumwa, koma Eliya anakwera pamwamba pa Phiri la Karimeli, ndipo anawerama mpaka pansi, nayika mutu wake pakati pa mawondo ake.
Eliya anawuza mtumiki wake kuti, “Pita kayangʼane ku nyanja.” Ndipo iye anapita nakayangʼana.
Mtumikiyo anati, “Kulibe kanthu.”
Kasanu nʼkawiri Eliya anati, “Pitanso.”
Ulendo wachisanu ndi chiwiri mtumikiyo anafotokoza kuti, “Taonani, kamtambo kakangʼono kokhala ngati dzanja la munthu kakutuluka ku nyanja.”
Pamenepo Eliya anati, “Pita, kamuwuze Ahabu kuti, ‘Konzani galeta lanu ndipo mutsike mvula isanakutsekerezeni.’ ”
Nthawi imeneyi nʼkuti kuthambo kutayamba kusonkhana mitambo yakuda, mphepo inawomba, mvula yamphamvu inagwa ndipo Ahabu anakwera galeta napita ku Yezireeli. Dzanja la Yehova linali pa Eliya ndipo atamangira lamba chovala chake, anathamanga ndi kumupitirira Ahabu mpaka kukhala woyamba kukafika ku Yezireeli.
Eliya Athawira ku Phiri la Horebu
Tsono Ahabu anawuza Yezebeli zonse zimene anachita Eliya ndi momwe anaphera aneneri onse ndi lupanga. Choncho Yezebeli anatuma mthenga kwa Eliya kuti akamuwuze kuti, “Milungu indilange, ndipo indilange koopsa, ngati mawa nthawi ngati yomwe ino sindidzakupha iwe monga unaphera aneneriwo.”
Eliya ataona zimenezi, ananyamuka nathawa kupulumutsa moyo wake. Atafika ku Beeriseba ku Yuda, anasiya mtumiki wake kumeneko, ndipo Eliyayo anayenda ulendo wa tsiku limodzi mʼchipululu. Anafika pa kamtengo ka tsache, nakhala pansi pa tsinde lake napemphera kuti afe. Iye anati, “Yehova, ine ndatopa nazo. Chotsani moyo wanga. Ineyo sindine wopambana makolo anga.” Ndipo Eliya anagona tulo tofa nato pa tsinde pa kamtengoko.
Ndipo taonani, mngelo anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye.” Eliya anayangʼana, ndipo taonani kumutu kwake kunali buledi wootcha pa makala ndi botolo la madzi. Iye anadya ndi kumwa, nʼkugonanso.
Mngelo wa Yehova anabweranso kachiwiri, anamukhudza, namuwuza kuti, “Dzuka udye, popeza ulendowu ndi wautali.” Tsono Eliya anadzuka nadya ndi kumwa. Atapeza mphamvu chifukwa cha chakudyacho, anayenda masiku 40, usana ndi usiku mpaka anafika ku Horebu, phiri la Mulungu. Kumeneko analowa mʼphanga, nakhala komweko.
Ambuye Aonekera Eliya
Ndipo taonani, Yehova anayankhula naye kuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
Yehova anati, “Tuluka ndipo ukayime pa phiri pamaso pa Yehova, pakuti Yehova ali pafupi kudutsa pamenepo.”
Tsono mphepo yayikulu ndi yamphamvu inawomba ningʼamba mapiri ndi kuswa matanthwe pamaso pa Yehova, koma Yehova sanali mʼmphepomo. Itapita mphepoyo panachita chivomerezi, koma Yehova sanali mʼchivomerezicho. Chitapita chivomerezicho, panafika moto, koma Yehova sanali mʼmotomo. Ndipo utapita motowo, panamveka kamphepo kayaziyazi. Eliya atamva kamphepoko, anakokera chovala chake naphimba kumutu. Anatuluka ndipo anayima pa khomo la phanga.
Ndipo panamveka mawu akuti, “Eliya, ukuchita chiyani kuno?”
Iye anayankha kuti, “Ndakhala wodzipereka kwambiri kwa Yehova Mulungu Wamphamvuzonse. Aisraeli asiya pangano lanu, agwetsa maguwa anu ansembe, ndipo apha aneneri anu ndi lupanga. Ndatsala ine ndekha ndipo tsopano akufuna kundipha.”
Yehova anati kwa Eliyayo, “Bwerera njira imene unadzera, ndipo upite ku Chipululu cha ku Damasiko. Ukakafika kumeneko, ukadzoze Hazaeli kuti akhale mfumu ya ku Aramu. Ukadzozenso Yehu mwana wa Nimisi kuti akhale mfumu ya Israeli, ndiponso ukadzoze Elisa mwana wa Safati wa ku Abeli-Mehola kuti akhale mneneri wolowa mʼmalo mwako. Yehu adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Hazaeli, ndipo Elisa adzapha aliyense amene adzapulumuke ku lupanga la Yehu. Komabe ndasunga anthu 7,000 ku Israeli, anthu onse amene mawondo awo sanagwadirepo Baala, onse amene pakamwa pawo sipanapsompsoneko fano lake.”
Kuyitanidwa kwa Elisa
Kotero Eliya anachoka kumeneko, nakapeza Elisa mwana wa Safati. Iye ankatipula ndi mapulawo khumi ndi awiri okokedwa ndi ngʼombe ziwiriziwiri zapamagoli, ndipo iye mwini ankayendetsa goli la khumi ndi chiwiri. Eliya anapita kumene anali namuveka chofunda chake. Pomwepo Elisa anasiya ngʼombe zake nathamangira Eliya. Iye anati, “Mundilole kuti ndikatsanzike abambo ndi amayi anga, ndipo kenaka ndidzakutsatani.”
Eliya anayankha kuti, “Bwerera. Ine ndachita chiyani kwa iwe?”
Choncho Elisa anamusiya Eliyayo nabwerera kwawo. Anatenga ngʼombe zake ziwiri zapagoli nazipha. Anatenga magoli a mapulawo ake nasonkhera moto kuphikira nyamayo ndipo anayipereka kwa anthu kuti adye. Ndipo ananyamuka natsatira Eliya ndi kukhala mtumiki wake.
Beni-Hadadi Athira Nkhondo Samariya
Tsono Beni-Hadadi mfumu ya ku Aramu inasonkhanitsa magulu ake onse a ankhondo. Iye pamodzi ndi mafumu 32, akavalo awo ndi magaleta awo, anapita kukawuzungulira mzinda wa Samariya ndi kuwuthira nkhondo. Iye anatuma amithenga ake mu mzindamo kwa Ahabu mfumu ya Israeli, kukanena kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Siliva wako ndi golide wako ndi wanga, ndipo akazi ako okongola ndi ana ako ndi anganso.’ ”
Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Monga mmene mwanenera, mbuye wanga mfumu, ine pamodzi ndi zonse zomwe ndili nazo ndi zanu.”
Amithenga aja anabwereranso kwa Ahabu ndipo anamuwuza kuti, “Beni-Hadadi akuti, ‘Ine ndinakulamula kuti undipatse siliva wako ndi golide wako, akazi ako ndi ana ako. Koma mawa nthawi ngati yomwe ino ndidzatuma atumiki anga kudzafufuza mʼnyumba yako yaufumu ndi nyumba za akuluakulu ako. Iwo adzatenga chilichonse chimene umachidalira ndi kupita nacho.’ ”
Pamenepo mfumu ya Israeli inayitanitsa akuluakulu a mʼdzikomo niwawuza kuti, “Taonani momwe munthuyu akufunira kutibweretsera mavuto! Atatumiza mawu oti ndimupatse akazi anga ndi ana anga, siliva wanga ndi golide wanga, ine sindinamukanize.”
Akuluakulu onse ndi anthu onse anayankha kuti, “Musamumvere kapena kuvomereza zofuna zake.”
Tsono Ahabu anayankha amithenga a Beni-Hadadi kuti, “Kamuwuzeni mbuye wanga mfumu kuti, ‘Mtumiki wanu adzachita zonse zimene munazifuna nthawi yoyamba ija, koma izi mwazifunazi sindingazikwanitse.’ ” Iwo anachoka nakapereka yankho kwa Beni-Hadadi.
Pamenepo Beni-Hadadi anatumizanso uthenga wina kwa Ahabu kuti, “Milungu indilange koopsa, ngati mu Samariya mudzakhale fumbi loti nʼkudzaza dzanja la aliyense wa anthu anga.”
Mfumu ya Israeli inayankha kuti, “Kamuwuzeni kuti, ‘Mwamuna mnzako nʼpachulu, nʼkulinga utakwerapo.’ ”
Beni-Hadadi anamva uthenga umenewu pamene iye ankamwa ndi mafumu anzake mʼmatenti awo, ndipo analamula anthu ake kuti, “Konzekerani kukathira nkhondo.” Choncho anakonzekera kukathira nkhondo mzindawo.
Ahabu Agonjetsa Beni-Hadadi
Ndipo taonani, mneneri wina anabwera kwa Ahabu mfumu ya Israeli nadzalengeza kuti, “Yehova akuti, ‘Kodi ukuchiona chigulu chachikulu cha ankhondochi? Taona, ndikuchipereka chimenechi lero mʼdzanja lako, ndipo pamenepo udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Ahabu anafunsa kuti, “Koma ndani adzachita zimenezi?”
Mneneri anayankha kuti, “Yehova akuti, ‘Adzachita zimenezi ndi asilikali a nduna za mʼzigawo.’ ”
Ndipo iye anafunsa kuti, “Kodi ndani adzayambe nkhondoyi?”
Mneneriyo anayankha kuti, “Ndinu.”
Choncho Ahabu anawerenga asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndipo onse analipo 232. Ndipo anawerenganso ankhondo a ku Israeli ndipo onse analipo 7,000. Iwo ananyamuka nthawi yamasana pamene Beni-Hadadi ndi mafumu 32 othandizana naye ankamwa mpaka kuledzera mʼmatenti awo. Asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo ndiwo amene anayamba kupita ku nkhondo.
Nthawi imeneyi Beni-Hadadi nʼkuti atatumiza anthu oti akazonde, amene anadzafotokoza kuti, “Anthu ankhondo akubwera kuchokera ku Samariya.”
Iye anati, “Kaya akubwera mwamtendere kapena mwankhondo, muwagwire amoyo.”
Choncho asilikali achinyamata a nduna za mʼzigawo anatuluka mu mzinda, gulu lankhondo lili pambuyo pawo. Ndipo aliyense wa iwo anapha munthu wake. Ataona izi, Aaramu anathawa Aisraeli ali pambuyo pawo kuwapirikitsa. Koma Beni-Hadadi mfumu ya ku Aaramu anathawa atakwera pa kavalo pamodzi ndi ankhondo ena okweranso pa akavalo. Mfumu ya Israeli inapita chitsogolo ndi kugwira akavalo ndi magaleta ndipo Aaramu ambiri anaphedwa.
Zitachitika izi, mneneri wina anabwera kwa mfumu ya Israeli ndipo anati, “Mulimbike ndipo muganize bwino zoti mudzachite, chifukwa chaka chikudzachi mfumu ya Aramu idzakuthiraninso nkhondo.”
Nthawi imeneyi, akuluakulu a mfumu ya Aramu anamulangiza kuti, “Milungu ya anthu a ku Israeli ndi milungu ya mʼmapiri. Nʼchifukwa chake anali ndi mphamvu zotipambana ife. Koma ngati tidzamenyana nawo ku chigwa, ndithudi ife tidzakhala ndi mphamvu kuposa iwo. Inu chitani izi: chotsani mafumu onse pa maudindo awo ndipo mʼmalo mwawo muyikemo atsogoleri a ankhondo. Musonkhanitsenso gulu lankhondo lofanana ndi lomwe linaphedwa lija, akavalo monga omwe anaphedwa aja, ndi magaleta monga omwe anawonongedwa aja, kuti tikamenyane ndi Israeli ku chigwa. Pamenepo, ife tidzapambana iwowo.” Beni-Hadadi anagwirizana nawo ndipo anachita momwemo.
Chaka chinacho Beni-Hadadi anasonkhanitsa Aaramu, napita ku Afeki kukamenyana ndi Israeli. Aisraeli atasonkhananso, napatsidwa zakudya zawo anapita kukakumana nawo. Aisraeli anamanga misasa yawo moyangʼanana ndi Aaramu ndipo ankaoneka ngati timagulu tiwiri ta mbuzi, pomwe Aaramu anali atakuta dera lonselo.
Munthu wa Mulungu anabwera, nawuza mfumu ya Israeli kuti, “Yehova akuti, ‘Popeza Aaramu akuganiza kuti Yehova ndi mulungu wa ku mapiri, osati wa ku zigwa, Ine ndidzapereka chigulu chonsechi kwa iwe, ndipo iwe udzadziwa kuti Ine ndine Yehova.’ ”
Kwa masiku asanu ndi awiri anakhala moyangʼanana mʼmisasa yawo, ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri nkhondo inayambika. Aisraeli anapha Aaramu okwana 100,000 tsiku limodzi lokha. Ena onse otsala anathawira ku Afeki, kumene khoma linagwera anthu 27,000. Ndipo Beni-Hadadi anathawira mu mzinda, nakabisala mʼchipinda chamʼkati.
Atumiki ake anamuwuza kuti, “Taonani, ife tamva kuti mafumu a fuko la Israeli ndi achifundo. Tiyeni tipite kwa mfumu ya ku Israeli titavala ziguduli mʼchiwuno mwathu ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwathu. Mwina iye sakakuphani.”
Atavala ziguduli mʼchiwuno mwawo ndi kumanga zingwe mʼmakosi mwawo, anapita kwa mfumu ya ku Israeli ndipo anayiwuza kuti, “Mtumiki wanu Beni-Hadadi akunena kuti, ‘Chonde loleni kuti ndikhale moyo.’ ”
Mfumu inayankha kuti, “Kodi iye akanali ndi moyo? Iye ujatu ndi mʼbale wanga.”
Anthuwo ankaganiza kuti mawuwo anali abwino ndipo anavomereza mawuwa mofulumira. Iwo anati, “Inde, Beni-Hadadi ndi mʼbale wanu!”
Mfumu inati, “Pitani kamutengeni.” Beni-Hadadi atatuluka, Ahabu anamukweza mʼgaleta lake.
Beni-Hadadi anawuza Ahabu kuti, “Ndidzabweza mizinda imene abambo anga analanda abambo anu. Ndipo mutha kumanga nyumba zanu zamalonda mu Damasiko, monga anachitira abambo anga ku Samariya.”
Ahabu anati, “Chifukwa cha mgwirizano umenewu, ine ndidzakumasula.” Choncho anachita naye mgwirizano, ndipo anamulola kuti apite.
Mneneri Adzudzula Ahabu
Molamulidwa ndi Yehova, mmodzi mwa ana a aneneri anawuza mnzake kuti, “Chonde, menye ndi chida chako,” koma mnzakeyo anakana.
Choncho mneneriyo anati, “Chifukwa sunamvere Yehova, ukangochoka pano, mkango ukupha.” Ndipo munthuyo atangochoka pamenepo, mkango unamupeza ndi kumupha.
Mneneriyo anapeza munthu wina ndipo anamuwuza kuti, “Chonde, menye.” Choncho munthuyo anamumenya ndi kumuvulaza. Pamenepo mneneriyo anapita nakayima pa msewu kudikirira mfumu. Iye anadzibisa nakulunga nsalu nkhope yake. Mmene mfumu inkadutsa pamenepo, mneneriyo anafuwula kwa mfumuyo kuti, “Ine mtumiki wanu ndinalowa pakati pa nkhondo, ndipo munthu wina anabwera kwa ine atatenga mmodzi mwa anthu ogwidwa pa nkhondo, nandiwuza kuti, ‘Sunga munthu uyu. Ngati asowa, ndiye kuti ndidzakupha, kapena udzalipira ndalama 3,000 za siliva.’ Pamene ine mtumiki wanu ndinali wotanganidwa apa ndi apa, munthuyo anasowa.”
Mfumu ya Israeli inati, “Chimenechi ndiye chilango chako. Iwe wadziweruza wekha.”
Pamenepo mneneriyo anachotsa msangamsanga nsalu yomwe anakulunga pa nkhope yake, ndipo mfumu ya Israeli inamuzindikira kuti ndi mmodzi mwa aneneri. Iye anawuza mfumu kuti, “Yehova akuti, ‘Chifukwa chakuti mwamasula munthu amene Ine ndinati ndi woyenera kuphedwa, inuyo ndi amene mudzaphedwe mʼmalo mwa iyeyo, anthu anu mʼmalo mwa anthu ake.’ ” Mwachisoni ndi mokwiya, mfumu ya Israeli inapita ku nyumba yake yaufumu ku Samariya.
Munda Wamphesa wa Naboti
Zitatha izi, panachitika nkhani yokhudza Naboti wa ku Yezireeli amene anali ndi munda wamphesa ku Yezireeli, pafupi ndi nyumba ya mfumu Ahabu, mfumu ya ku Samariya. Ahabu anawuza Naboti kuti, “Patse munda wako wa mpesa kuti ukhale munda wanga wa ndiwo zamasamba, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga yaufumu. Mosinthana ndi mundawu ndidzakupatsa wina wabwino, kapena ngati ungafune, ndidzakupatsa ndalama pa mtengo wake wa mundawu.”
Koma Naboti anayankha Ahabu kuti, “Pali Yehova, sindingakupatseni cholowa cha makolo anga.”
Pamenepo Ahabu anapita ku nyumba yake, wachisoni ndi wokwiya chifukwa Naboti wa ku Yezireeli anamuwuza kuti, “Sindidzakupatsani cholowa cha makolo anga.” Ahabu anakagona pa bedi lake atayangʼana kumbali ndipo anakana chakudya.
Yezebeli mkazi wake analowa ndipo anamufunsa kuti, “Chifukwa chiyani mukuoneka achisoni? Chifukwa chiyani simukufuna chakudya?”
Ahabu anayankha mkazi wake kuti, “Chifukwa chake nʼchakuti ine ndinamuwuza Naboti wa ku Yezireeli kuti, ‘Gulitse munda wako wa mpesa kapena ngati ungakonde ine ndidzakupatsa munda wina wabwino mʼmalo mwake.’ Koma iye anandiyankha kuti, ‘Sindidzakupatsani munda wanga wa mpesa.’ ”
Ndipo Yezebeli mkazi wake anati, “Kodi umu ndi mmene mumachitira ngati mfumu ya Israeli? Dzukani, idyani! Sangalalani. Ine ndidzakutengerani munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli.”
Choncho Yezebeli analemba makalata mʼdzina la Ahabu, nawadinda chidindo cha mfumu, nawatumiza makalatawo kwa akuluakulu ndi kwa anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake. Mʼmakalatamo Yezebeli analemba kuti:
“Lengezani kuti anthu asale chakudya ndipo muyike Naboti pa malo aulemu pakati pa anthu. Koma muyike anthu awiri oyipa mtima moyangʼanana naye ndipo iwo achitire umboni kuti watemberera Mulungu ndiponso mfumu. Ndipo mumutulutse ndi kumuponya miyala ndi kumupha.”
Choncho akuluakulu ndi anthu olemekezeka amene ankakhala ndi Naboti mu mzinda mwake anachita monga analamulira Yezebeli mʼmakalata amene anawalembera. Iwo analengeza kuti anthu asale chakudya ndipo anayika Naboti pa malo aulemu pakati pa anthu. Ndipo anthu awiri oyipa anabwera nakhala moyangʼanana naye ndipo anamunenera zoyipa Naboti pamaso pa anthu, ponena kuti, “Naboti watemberera Mulungu ndiponso mfumu.” Choncho anamutulutsira kunja kwa mzinda ndi kumuponya miyala ndi kumupha. Atatero anatumiza mawu kwa Yezebeli akuti, “Naboti amuponya miyala ndipo wafa.”
Yezebeli atangomva kuti Naboti amuponya miyala ndipo wafa, iye anakamuwuza Ahabu kuti, “Dzukani, katengeni munda wamphesa wa Naboti wa ku Yezireeli umene anawukaniza kukugulitsani. Naboti sali moyonso, koma wafa.” Ahabu atamva kuti Naboti wafa, ananyamuka kukatenga munda wamphesa wa Naboti.
Ndipo Yehova anayankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti, “Nyamuka, pita ukakumane ndi Ahabu, mfumu ya Israeli amene amalamulira ku Samariya. Pano ali ku munda wamphesa wa Naboti kumene wapita kuti akatenge mundawo kuti ukhale wake. Ukamuwuze kuti: ‘Yehova akuti, Kodi siwapha munthu ndi kumulandanso munda wake?’ Ndipo ukamuwuzenso kuti, ‘Yehova akuti, Pamalo pamene agalu ananyambita magazi a Naboti, pamalo pomwepo agalu adzanyambita magazi ako, inde, akonso!’ ”
Ahabu anati kwa Eliya, “Tsono wandipeza, iwe mdani wanga!”
Eliya anayankha kuti, “Inde ndakupezani chifukwa mwadzigulitsa kuti muchite zoyipa pamaso pa Yehova. Iye akuti ‘Taonani, ine ndidzabweretsa mavuto pa iwe. Ndidzawononga kotheratu zidzukulu zako ndi kuchotsa mu Israeli munthu aliyense wamwamuna wa banja la Ahabu, kapolo kapena mfulu. Ndidzawononga nyumba yako monga momwe ndinawonongera nyumba ya Yeroboamu mwana wa Nebati ndiponso ngati nyumba ya Baasa mwana wa Ahiya, chifukwa wandikwiyitsa Ine ndi kuchimwitsa Israeli.’
“Ndipo kunena za Yezebeli, Yehova akuti, ‘Agalu adzadya Yezebeli mʼmbali mwa khoma la Yezireeli.’
“Agalu adzadya munthu aliyense wa nyumba ya Ahabu amene adzafere mu mzinda, ndipo mbalame za mu mlengalenga zidzadya aliyense wofera ku thengo.”
(Kunalibe munthu ngati Ahabu, amene anadzigulitsa kuchita zoyipa pamaso pa Yehova, amene anakopedwa ndi mkazi wake Yezebeli. Iye anachita zonyansa kwambiri popembedza mafano, monga mmene ankachitira Aamori amene Yehova anawachotsa pamene Aisraeli ankafika).
Ahabu atamva mawu amenewa, anangʼamba zovala zake, navala ziguduli ndi kusala chakudya. Anagona pa ziguduli, nayenda pangʼonopangʼono.
Pamenepo Yehova anayankhula ndi Eliya wa ku Tisibe kuti, “Kodi waona mmene Ahabu wadzichepetsera pamaso panga? Chifukwa wadzichepetsa, sindidzabweretsa mavuto amenewa pa nthawi ya moyo wake, koma ndidzawabweretsa pa nyumba yake pa nthawi ya mwana wake.”
Mikaya Anenera Motsutsa Ahabu
Kwa zaka zitatu panalibe nkhondo pakati pa Aramu ndi Israeli. Koma pa chaka chachitatu, Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita kukacheza ndi mfumu ya ku Israeli. Mfumu ya ku Israeli nʼkuti itawuza atumiki ake kuti, “Kodi inu simukudziwa kuti Ramoti Giliyadi ndi dera lathu ndipo ife palibe chimene tikuchita kuti tilitenge deralo mʼmanja mwa mfumu ya Aramu?”
Tsono iye anafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane ku nkhondo ku Ramoti Giliyadi?”
Yehosafati anayankha mfumu ya ku Israeli kuti, “Ine ndili monga inu, anthu anga monga anthu anu, akavalo anga monga akavalo anu.” Koma Yehosafati anawuzanso mfumu ya ku Israeli kuti, “Poyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.”
Choncho mfumu ya Israeli inasonkhanitsa pamodzi aneneri okwanira 400, ndipo inawafunsa kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena ndileke?”
Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Ambuye waupereka mzindawo mʼmanja mwa mfumu.”
Koma Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi kuno kulibenso mneneri wina wa Yehova kumene ife tingakafunsireko nzeru?”
Mfumu ya ku Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife tingakafunsire kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa iyeyo samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa nthawi zonse. Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.”
Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu musatero.”
Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa atumiki ake ndipo inati, “Kayitane Mikaya mwana wa Imula msangamsanga.”
Atavala mikanjo yawo yaufumu, mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopondera tirigu pafupi ndi chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo. Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’ ”
Aneneri ena onse ananenera zomwezonso. Iwo anati, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
Wamthenga amene anapita kukayitana Mikaya anamuwuza kuti, “Taonani, aneneri onse monga munthu mmodzi akunenera za kupambana kwa mfumu. Mawu anunso akhale ogwirizana ndi mawu awo, ndipo mukayankhule zabwino.”
Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndikawawuza zokhazo zimene Yehova akandiwuze.”
Atafika, Ahabu anamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena tileke?”
Iye anayankha kuti, “Pitani ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.”
Ahabu anati kwa iye, “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti undiwuze zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?”
Pamenepo Mikaya anayankha kuti, “Ndinaona Aisraeli onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mwamtendere.’ ”
Mfumu ya ku Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti ameneyu samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa zokhazokha?”
Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere. Ndipo Yehova anati, ‘Kodi ndani amene akamukope Ahabu kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi, nʼkukafera komweko?’ ”
“Wina anapereka maganizo ena ndipo winanso maganizo ena. Potsirizira, mzimu wina unabwera ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, ‘Ine ndidzamukopa.’ ”
Yehova anafunsa kuti, “Ukamukopa bwanji?”
Mzimuwo unati, “Ndidzapita ndi kukakhala mzimu wabodza pakamwa pa aneneri ake onse.”
Yehova anati, “ ‘Iwe udzamukopadi. Pita kachite zomwezo.’
“Ndipo tsopano taonani, Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anu onsewa. Yehova waneneratu kuti mukaona mavuto.”
Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi namenya Mikaya patsaya. Iye anafunsa Mikaya kuti, “Kodi mzimu wa Yehova unadzera njira iti pamene umatuluka mwa ine kuti uziyankhula ndi iwe?”
Mikaya anayankha kuti, “Udzaona pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.”
Pamenepo mfumu ya ku Israeli inalamula kuti, “Mugwireni Mikaya ndipo mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyikeni mʼndende munthu uyu ndipo musamupatse chakudya china koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwerera mwamtendere.’ ”
Mikaya ananena kuti, “Ngati mudzabwerera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo iye anapitiriza kunena kuti, “Gwiritsitsani mawu angawa, anthu inu nonse!”
Ahabu Aphedwa ku Ramoti Giliyadi
Choncho mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi. Mfumu ya ku Israeli inawuza Yehosafati kuti, “Ine ndidzalowa mu nkhondoyi modzibisa, koma inu muvale zovala zanu zaufumu.” Choncho mfumu ya ku Israeli inadzibisa ndi kupita ku nkhondo.
Tsono mfumu ya ku Aramu nʼkuti italamulira anthu ake 32 olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israeli.” Olamulira magaleta ataona Yehosafati, ankaganiza kuti, “Ndithu iyi ndiye mfumu ya ku Israeli.” Choncho anabwerera kukamenyana naye, koma Yehosafati atafuwula, olamulira akavalo anaona kuti sanali mfumu ya ku Israeli ndipo analeka kumuthamangitsa.
Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndi kulasa mfumu ya ku Israeli polumikizira malaya ake odzitetezera. Mfumu inawuza woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka ndipo undichotse pa nkhondo pano pakuti ndalasidwa.” Nkhondo inakula kwambiri tsiku limenelo, ndipo mfumu inakhala tsonga mʼgaleta lake moyangʼanana ndi Aaramu. Magazi ake ankayenderera pansi kuchokera mʼgaleta, ndipo pa nthawi ya madzulo inamwalira. Pamene dzuwa linkalowa, kunamveka mfuwu wa nkhondo kuti, “Munthu aliyense apite ku mzinda wa kwawo, aliyense apite ku dziko la kwawo!”
Ndipo mfumu ija inafa, nabwera nayo ku Samariya, ndipo anayika mʼmanda kumeneko. Anatsuka galeta lija pa dziwe la ku Samariya (pamene ankasamba akazi achiwerewere) ndipo agalu ananyambita magazi a mfumuyo, monga momwe Yehova ananenera.
Tsono ntchito zina za Ahabu, kuphatikiza zonse anazichita, nyumba yaufumu imene anamanga yokutidwa ndi minyanga ya njovu, mizinda yotetezedwa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli? Ahabu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Yehosafati Mfumu ya ku Yuda
Yehosafati, mwana wa Asa anakhala mfumu ya ku Yuda chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya ku Israeli. Yehosafati anali wa zaka 35 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Amayi ake anali Azuba mwana wa Silihi. Pa zinthu zonse, Yehosafati anayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanachite zotsutsana ndi machitidwe a abambo ake. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova. Komabe, malo azipembedzo sanawawononge, ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko. Yehosafati anakhala mwamtendere ndi mfumu ya ku Israeli.
Ntchito zake zina za Yehosafati, zinthu zimene anachita ndi zamphamvu zimene anaonetsa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Yuda? Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zachiwerewere mwa chipembedzo amene anatsalira pa nthawi ya ulamuliro wa Asa, abambo ake. Nthawi imeneyo kunalibe mfumu ku Edomu, amene ankalamulira anali munthu woyikidwa ndi mfumu ya ku Yuda.
Yehosafati anapanga sitima zapamadzi zopita ku Ofiri kukatenga golide, koma sitimazo sizinayende chifukwa zinawonongeka ku Ezioni Geberi. Nthawi imeneyo Ahaziya mwana wa Ahabu anawuza Yehosafati kuti, “Anthu anga ayende pa madzi pamodzi ndi anthu anu,” koma Yehosafati anakana.
Ndipo Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.
Ahaziya Mfumu ya ku Israeli
Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, chifukwa anayenda mʼnjira za abambo ndi amayi ake komanso mʼnjira za Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli. Potumikira ndi kupembedza Baala, iye anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli, monga momwe anachitira abambo ake.