- Biblica® Open God’s Word in Contemporary Chichewa 2016 1 MBIRI 1 Mbiri 1 Mbiri 1 Mbi 1 Mbiri Mbiri ya Makolo Kuchokera pa Adamu Mpaka pa Abrahamu Mpaka pa Ana a Nowa Adamu, Seti, Enosi Kenani, Mahalaleli, Yaredi, Enoki, Metusela, Lameki, Nowa. Ana a Nowa, Semu, Hamu ndi Yafeti. Fuko la Yafeti Ana aamuna a Yafeti anali: Gomeri, Magogi, Madai, Yavani, Tubala, Mesaki ndi Tirasi. Ana aamuna a Gomeri anali: Asikenazi, Rifati ndi Togarima Ana aamuna a Yavani anali: Elisa, Tarisisi, Kitimu ndi Rodanimu. Fuko la Hamu Ana aamuna a Hamu anali: Kusi, Miziraimu, Puti ndi Kanaani Ana aamuna a Kusi anali: Seba, Havila, Sabita, Raama ndi Sabiteka Ana aamuna a Raama anali: Seba ndi Dedani. Kusi anali abambo a Nimurodi amene anali wankhondo wamphamvu kwambiri pa dziko lapansi. Igupto ndiye kholo la Aludi, Aanami, Alehabu, Anafutu, Apaturusi, Akasilu (kumene kunachokera Afilisti) ndi Akafitori. Kanaani anabereka mwana wake wachisamba Sidoni, ndipo anaberekanso Ahiti, Ayebusi, Aamori, Agirigasi Ahivi, Aariki, Asini Aaravadi, Azemari ndi Ahamati. Fuko la Semu Ana aamuna a Semu anali: Elamu, Asuri, Aripakisadi, Ludi ndi Aramu. Ana aamuna a Aramu anali: Uzi, Huri, Geteri ndi Mesaki. Aripakisadi anabereka Sela ndipo Selayo anabereka Eberi: Eberi anabereka ana aamuna awiri: wina anamutcha Pelegi, chifukwa pa nthawiyo anthu a pa dziko lapansi anagawikana. Dzina la mʼbale wake linali Yokitani. Yokitani anabereka Alimodadi, Selefi, Hazari-Maveti, Yera, Hadoramu, Uzali, Dikila Obali, Abimaeli, Seba, Ofiri, Havila ndi Yobabu. Onsewa anali ana aamuna a Yokitani. Semu, Aripakisadi, Sela Eberi, Pelegi, Reu Serugi, Nahori, Tera ndi Abramu (amene ndi Abrahamu). Banja la Abrahamu Ana a Abrahamu ndi awa: Isake ndi Ismaeli. Zidzukulu za Hagara Zidzukulu zake zinali izi: Nebayoti ndiye anali mwana woyamba wa Ismaeli, kenaka Kedara, Adibeeli, Mibisamu, Misima, Duma, Masa, Hadadi, Tema, Yeturi, Nafisi ndi Kedema. Awa anali ana a Ismaeli. Zidzukulu za Ketura Ana a Ketura mzikazi wa Abrahamu anali awa: Zimurani, Yokisani, Medani, Midiyani, Isibaki ndi Suwa. Ana a Yokisani ndi awa: Seba ndi Dedani Ana aamuna a Midiyani anali, Efai, Eferi, Hanoki, Abida ndi Elida. Onsewa anali zidzukulu za Ketura. Zidzukulu za Sara Abrahamu anabereka Isake. Ana a Isake anali awa: Esau ndi Israeli. Ana a Esau Ana aamuna a Esau anali awa: Elifazi, Reueli, Yeusi, Yolamu ndi Kora. Ana a Elifazi anali awa: Temani, Omari, Zefo, Gatamu ndi Kenazi: Amene anabereka ndi Timna: Amaleki. Ana a Reueli anali awa: Nahati, Zera, Sama ndi Miza. Anthu a ku Seiri ku Edomu Ana a Seiri anali awa: Lotani, Sobala, Zibeoni, Ana, Disoni, Ezeri ndi Disani. Ana aamuna a Lotani anali awa: Hori ndi Homamu. Timna anali mlongo wake wa Lotani. Ana aamuna a Sobala anali awa: Alivani, Manahati, Ebala, Sefo ndi Onamu. Ana aamuna a Zibeoni anali awa: Ayiwa ndi Ana. Mwana wa Ana anali Disoni. Ana a Disoni anali awa: Hemudani, Esibani, Itirani ndi Kerani Ana aamuna a Ezeri anali awa: Bilihani, Zaavani ndi Yaakani. Ana aamuna a Disani anali awa: Uzi ndi Arani. Mafumu a ku Edomu Awa ndi mafumu amene ankalamulira dziko la Edomu, mfumu iliyonse ya Israeli isanayambe kulamulira kumeneko: Bela mwana wa Beori, mzinda wake ankawutcha Dinihaba. Bela atamwalira, Yobabu mwana wa Zera wochokera ku Bozira analowa ufumu mʼmalo mwake. Yobabu atamwalira, Husamu wochokera ku dziko la Atemani, analowa ufumu mʼmalo mwake. Husamu atamwalira, Hadadi mwana wa Bedadi, amene anagonjetsa Amidiyani mʼdziko la Mowabu, analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Aviti. Hadadi atamwalira, Samila wochokera ku Masireka analowa ufumu mʼmalo mwake. Samila atamwalira, Sauli wochokera ku Rehoboti wa ku Mtsinje analowa ufumu mʼmalo mwake. Sauli atamwalira, Baala-Hanani mwana wa Akibori analowa ufumu mʼmalo mwake. Pamene Baala-Hanani anamwalira, Hadadi analowa ufumu mʼmalo mwake. Mzinda wake unkatchedwa Pau, ndipo dzina la mkazi wake linali Mehatabeli mwana wa Matiredi, mwana wamkazi wa Me-Zahabu. Hadadi anamwaliranso. Mafumu a ku Edomu anali: Timna, Aliva, Yeteti, Oholibama, Ela, Pinoni, Kenazi, Temani, Mibezari, Magidieli ndi Iramu. Awa anali mafumu a ku Edomu. Ana a Israeli Ana a Israeli anali awa: Rubeni, Simeoni, Levi, Yuda, Isakara, Zebuloni, Dani, Yosefe, Benjamini, Nafutali, Gadi ndi Aseri. Yuda Mpaka pa Ana a Hezironi Ana a Hezironi Ana a Yuda anali awa: Eri, Onani ndi Sela. Ana atatu awa anabereka ndi mkazi wa Chikanaani, Batisuwa. Eri, mwana woyamba wa Yuda anali woyipa kwambiri pamaso pa Yehova, kotero Yehova anamupha. Mpongozi wake Tamara anamuberekera Perezi ndi Zera. Ana onse a Yuda analipo asanu. Ana a Perezi anali awa: Hezironi ndi Hamuli. Ana a Zera anali awa: Zimuri, Etani, Hemani, Kalikoli ndi Dara. Onse analipo asanu. Mwana wa Karimi anali Akani, amene anabweretsa mavuto pakati pa Israeli pamene anatenga zinthu zoyenera kuwonongedwa. Mwana wa Etani anali Azariya. Ana amene anabadwa kwa Hezironi anali: Yerahimeeli, Ramu ndi Kelubai. Kuchokera kwa Ramu Mwana wa Hezironi Ramu anabereka Aminadabu ndipo Aminadabu anali abambo ake a Naasoni, mtsogoleri wa fuko la Yuda. Naasoni anabereka Salima, Salima anabereka Bowazi, Bowazi anabereka Obedi ndipo Obedi anabereka Yese. Yese anabereka Eliabu mwana wake woyamba, wachiwiri Abinadabu, wachitatu Simea, wachinayi Netaneli, wachisanu Radai, wachisanu ndi chimodzi Ozemu ndi wachisanu ndi chiwiri Davide. Alongo awo anali Zeruya ndi Abigayeli. Ana atatu a Zeruya anali Abisai Yowabu ndi Asaheli. Abigayeli anali amayi ake a Amasa amene abambo ake anali Yeteri wa fuko la Ismaeli. Kalebe Mwana wa Hezironi Kalebe mwana wa Hezironi anabereka ana mwa Azuba mkazi wake (ndi mwa Yerioti). Ana a mkaziyo anali awa: Yeseri, Sobabu ndi Aridoni. Azuba atamwalira, Kalebe anakwatira Efurata, amene anamuberekera Huri. Huri anabereka Uri ndipo Uri anabereka Bezaleli. Patapita nthawi, Hezironi anagona ndi mwana wamkazi wa Makiri abambo ake a Giliyadi (iye anamukwatira ali ndi zaka 60) ndipo anamuberekera Segubu. Segubu anabereka Yairi, amene anali ndi mizinda 23 ku Giliyadi. (Koma Gesuri ndi Aramu analanda Havoti Yairi komanso Kenati ndi madera ake onse ozungulira, mizinda makumi asanu ndi umodzi). Onsewa anali adzukulu, a Makiri abambo ake a Giliyadi. Atamwalira Hezironi ku Kalebe Efurata, Abiya mkazi wa Hezironi anamuberekera Asihuri abambo a Tekowa. Yerahimeeli Mwana wa Hezironi Ana a Yerahimeeli, mwana woyamba wa Hezironi anali: Ramu, mwana wake woyamba, Buna, Oreni, Ozemu ndi Ahiya. Yerahimeeli anali ndi mkazi wina amene dzina lake linali Atara, amene anali amayi a Onamu. Ana a Ramu, mwana woyamba wa Yerahimeeli, anali awa: Maazi, Yamini ndi Ekeri. Ana a Onamu anali awa: Shamai ndi Yada. Ana a Shamai anali awa: Nadabu ndi Abisuri. Mkazi wa Abisuri anali Abihaili, amene anamuberekera Ahibani ndi Molidi. Ana a Nadabu anali awa: Seledi ndi Apaimu. Koma Seledi anamwalira wopanda ana. Ana a Apaimu anali awa: Isi, amene anabereka Sesani. Sesani anabereka Ahilai. Ana a Yada, mʼbale wa Samai, anali awa: Yereri ndi Yonatani. Koma Yeteri anamwalira wopanda ana. Ana a Yonatani anali awa: Peleti ndi Zaza. Amenewa anali adzukulu a Yerahimeeli. Sesani sanabereke ana aamuna koma aakazi okhaokha. Iye anali ndi wantchito wa ku Igupto, dzina lake Yariha. Sesani anapereka mwana wake wamkazi kwa Yariha wantchito wake kuti amukwatire ndipo anamuberekera Atayi. Atayi anali abambo ake a Natani, Natani anali abambo ake a Zabadi, Zabadi anali abambo a Efilali, Efilali anali abambo a Obedi, Obedi anali abambo a Yehu, Yehu anali abambo a Azariya, Azariya anali abambo a Helezi, Helezi anali abambo a Eleasa, Eleasa anali abambo ake a Sisimai, Sisimai anali abambo a Salumu, Salumu anali abambo a Yekamiya, Yekamiya anali abambo a Elisama. Mabanja a Kalebe Ana a Kalebe mʼbale wa Yerahimeeli anali awa: Mesa mwana wachisamba, anali abambo a Zifi, ndipo mwana wake Maresa anali abambo a Hebroni. Ana a Hebroni anali awa: Kora, Tapuwa, Rekemu ndi Sema. Sema anali abambo ake Rahamu ndipo Rahamu anali abambo a Yorikeamu. Rekemu anali abambo a Samai. Mwana wa Samai anali Maoni, ndipo Maoni anali abambo a Beti Zuri. Efai, mzikazi wa Kalebe, anali amayi a Harani, Moza ndi Gazezi. Harani anali abambo a Gazezi. Ana a Yahidai anali awa: Regemu, Yotamu, Gesani, Peleti, Efai ndi Saafi. Maaka mzikazi wa Kalebe anali mayi Seberi ndi Tirihana. Iye anaberekanso Saafi abambo a Madimena ndi Seva abambo a Makibena ndi Gibeya. Mwana wamkazi wa Kalebe anali Akisa. Izi zinali zidzukulu za Kalebe. Ana a Huri mwana wachisamba wa Efurata anali awa: Sobala abambo a Kiriati Yearimu, Salima abambo a Betelehemu ndi Harefu abambo ake a Beti-Gadera. Zidzukulu za Sobala abambo a Kiriati Yearimu zinali izi: Harowe, theka la banja la Manahati, ndipo mabanja a Kiriati-Yeyarimu anali awa: Aitiri, Aputi, Asumati ndi Amisirai. Azorati ndi Aesitaoli anachokera kwa amenewa. Zidzukulu za Salima zinali izi: Betelehemu, Anetofati, Atiroti-Beti-Yowabu, theka la banja la Manahati, Azori, ndiponso mabanja a alembi amene amakhala ku Yabesi: Atiroti, Asimeati ndiponso Asukati. Awa ndi Akeni amene anachokera kwa Hamati, kholo la Arekabu. Ana a Davide Ana aamuna a Davide amene anabadwira ku Hebroni anali awa: Woyamba anali Amnoni, amayi ake anali Ahinoamu wa ku Yezireeli; wachiwiri anali Danieli, amayi ake anali Abigayeli wa ku Karimeli; wachitatu anali Abisalomu, mwana wa Maaka mwana wa Talimai mfumu ya Gesuri; wachinayi anali Adoniya amayi ake anali Hagiti; wachisanu anali Sefatiya, amayi ake anali Abitali; wachisanu ndi chimodzi anali Itireamu, amayi ake anali Egila. Ana asanu ndi mmodzi awa a Davide anabadwira ku Hebroni kumene analamulirako zaka zisanu ndi ziwiri ndi miyezi isanu ndi umodzi. Davide analamuliranso mu Yerusalemu kwa zaka 33, ndipo ana amene anabadwira ku Yerusalemuko anali awa: Samua, Sobabu, Natani ndi Solomoni. Ana anayi awa anali a Batisuwa mwana wa Amieli. Anaberekanso Ibihari, Elisua, Elipeleti, Noga, Nefegi, Yafiya, Elisama, Eliada ndi Elifeleti, onse analipo asanu ndi anayi. Onsewa anali ana a Davide, osawerengera ana a azikazi. Ndipo mlongo wawo anali Tamara. Mafumu a Yuda Mwana wa Solomoni anali Rehabiamu, Rehabiamu anabereka Abiya, Abiya anabereka Asa, Asa anabereka Yehosafati, Yehosafati anabereka Yehoramu, Yehoramu anabereka Ahaziya, Ahaziya anabereka Yowasi, Yowasi anabereka Amaziya, Amaziya anabereka Azariya, Azariya anabereka Yotamu, Yotamu anabereka Ahazi, Ahazi anabereka Hezekiya, Hezekiya anabereka Manase, Manase anabereka Amoni, Amoni anabereka Yosiya. Ana a Yosiya anali awa: Yohanani mwana wake woyamba, Yehoyakimu mwana wake wachiwiri, Zedekiya mwana wake wachitatu, Salumu mwana wake wachinayi. Ana a Yehoyakimu: Yekoniya ndi Zedekiya mwana wake. Mayina a Mafumu Utatha Ukapolo Zidzukulu za Yekoniya wa mʼndende zinali izi: mwana wake Silatieli, Malikiramu, Pedaya, Senazara, Yekamiya, Hosama ndi Nedabiya. Ana a Pedaya anali awa: Zerubabeli ndi Simei. Ana a Zerubabeli anali awa: Mesulamu ndi Hananiya. Mlongo wawo anali Selomiti. Panalinso ana ena asanu awa: Hasubu, Oheli, Berekiya, Hasabiya ndi Yusabu-Hesedi. Zidzukulu za Hananiya zinali izi: Pelatiya ndi Yesaiya, ndiponso ana a Refaya, ana a Arinani, ana a Obadiya ndi ana a Sekaniya. Zidzukulu za Sekaniya zinali izi: Semaya ndi ana ake: Hatusi, Igala, Bariya, Neariya ndi Safati. Onse anali asanu ndi mmodzi. Ana a Neariya anali awa: Eliyoenai, Hezekiya ndi Azirikamu. Onse anali atatu. Ana a Eliyoenai: Hodaviya, Eliyasibu, Pelaya, Akubu, Yohanani, Delaya ndi Anani, onse anali asanu ndi awiri. Mabanja Ena a Yuda Ana a Yuda anali awa: Perezi, Hezironi, Karimi, Huri ndi Sobali. Reaya mwana wa Sobala anabereka Yahati, ndipo Yahati anabereka Ahumai ndi Lahadi. Awa anali mabanja a Azorati. Ana a Etamu anali awa: Yezireeli, Isima ndi Idibasi. Dzina la mlongo wawo linali Hazeleliponi. Penueli anabereka Gedori, ndipo Ezeri anabereka Husa. Awa anali ana a Huri, mwana wachisamba wa Efurata ndi abambo a Betelehemu. Asihuri abambo a Tekowa anali ndi akazi awiri, Hela ndi Naara. Naara anamuberekera Ahuzamu, Heferi, Temani ndi Haahasitari. Awa ndiwo anali ana a Naara. Ana a Hela: Zereti, Zohari, Etinani, ndi Kozi, amene anali abambo ake a Anubi ndi Hazo-Beba ndi mabanja a Ahariheli mwana wa Harumi. Yabesi anali munthu wolemekezeka kwambiri kuposa abale ake. Amayi ake anamutcha Yabesi kutanthauza kuti, “Chifukwa ndinamubala ndi ululu wambiri.” Yabesi analira kwa Mulungu wa Israeli kuti, “Mundidalitse ndipo mukulitse dziko langa! Dzanja lanu likhale pa ine ndipo mundisunge kuti choyipa chisandigwere ndi kundisautsa.” Ndipo Mulungu anamupatsa chopempha chakecho. Kelubi, mʼbale wa Suha, anabereka Mehiri, amene anabereka Esitoni. Esitoni anabereka Beti-Rafa, Paseya ndi Tehina amene anabereka Iri Nahasi. Amenewa ndiwo anthu a ku Reka. Ana a Kenazi anali awa: Otanieli ndi Seraya. Ana a Otanieli anali awa: Hatati ndi Meonotai. Meonotai anabereka Ofura. Seraya anabereka Yowabu, amene anabereka Ge-Harasimu. Anawatcha dzina ili chifukwa anthu ake anali amisiri. Ana a Kalebe mwana wa Yefune anali awa: Iru, Ela ndi Naama. Mwana wa Ela anali Kenazi. Ana a Yehaleleli anali awa: Zifi, Zifa, Tiriya ndi Asareli. Ana a Ezara anali awa: Yeteri, Meredi, Eferi ndi Yaloni. Mmodzi mwa akazi a Meredi anabereka Miriamu, Samai ndi Isiba abambo ake a Esitemowa. (Mkazi wake wa Chiyuda anabereka Yaredi abambo ake a Gedori, Heberi abambo ake a Soko ndi Yekutieli abambo a Zanowa). Awa anali ana a mwana wamkazi wa Farao, Bitia, amene Meredi anakwatira. Ana a mkazi wa Hodiya, mlongo wa Nahamu anali awa: abambo ake a Keila wa ku Garimi ndi Esitemowa wa ku Maaka. Ana a Simeoni anali awa: Amnoni, Rina, Beni-Hanani ndi Tiloni. Ana a Isi anali awa: Zoheti ndi Beni-Zoheti. Ana a Sela mwana wa Yuda anali awa: Eri amene anabereka Leka, Laada amene anabereka Maresa ndi mabanja a anthu owomba nsalu zofewa ndi zosalala a ku Beti-Asibeya, Yokimu, anthu a ku Kozeba, ndiponso Yowasi ndi Sarafi, amene ankalamulira Mowabu ndi Yasibu-Lehemu. (Nkhani zimenezi ndi zakalekale). Iwo anali owumba mbiya amene ankakhala ku Netaimu ndi Gederi. Ankakhala kumeneko ndi kumatumikira mfumu. Simeoni Ana a Simeoni anali awa: Nemueli, Yamini, Yaribu, Zera ndi Sauli; Salumu anali mwana wa Sauli, Mibisamu anali mwana wa Salumu ndipo Misima anali mwana wa Mibisamu. Zidzukulu za Misima zinali izi: Hamueli, Zakuri ndi Simei. Simei anali ndi ana aamuna 16 ndi ana aakazi 6, koma abale ake sanabereke ana ambiri; kotero banja lawo silinakule ngati anthu ena a ku Yuda. Iwo amakhala ku Beeriseba, Molada, Hazari-Suwali, Biliha, Ezemu, Toladi, Betueli, Horima, Zikilagi, Beti-Marikaboti, Hazari-Susimu, Beti-Biri ndi Saaraimu. Iyi inali mizinda yawo mpaka pa nthawi ya ulamuliro wa Davide. Midzi yowazungulira inali Etamu, Aini, Rimoni, Tokeni ndi Asani, midzi isanu ndi midzi yonse yozungulira mizinda imeneyi mpaka ku Baala. Awa anali malo awo okhalapo. Ndipo anasunga mbiri ya makolo awo. Mesobabu, Yamuleki, Yosa mwana wa Amaziya, Yoweli, Yehu mwana wa Yosibiya, mwana wa Seraya, mwana wa Asieli, komanso Eliyoenai, Yaakoba, Yesohaya, Asaya, Adieli, Yesimieli, Benaya, ndiponso Ziza mwana wa Sifi, mwana wa Aloni, mwana wa Yedaya, mwana wa Simiri, mwana wa Semaya. Anthu amene atchulidwawa anali atsogoleri a mabanja awo. Mabanja awo anakula kwambiri ndipo anakafika ku malire a Gedori ku chigwa cha kummawa kufuna msipu wodyetsa ziweto zawo. Anapeza msipu wobiriwira ndi wabwino ndipo dziko linali lalikulu, la mtendere ndi bata. Kumeneko kunkakhala fuko la Hamu poyamba. Anthu amene mayina awowa alembedwa, anabwera pa nthawi ya Hezekiya mfumu ya Yuda. Iwo anathira nkhondo fuko la Hamu mʼmalo awo amene amakhala komanso Ameuni amene anali kumeneko ndipo anawononga onsewo kotero kuti mbiri yawo simvekanso mpaka lero lino. Kotero iwo anakhala mʼmalo awo chifukwa kunali msipu wa ziweto zawo. Ndipo anthu 500 a fuko la Simeoni, motsogozedwa ndi Pelatiya, Neariya, Refaya ndi Uzieli, ana a Isi, analanda dziko lamapiri la Seiri. Iwo anapha Aamaleki otsala amene anali atapulumuka ndipo akukhala kumeneko mpaka lero lino. Fuko la Rubeni Ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli (iye anali woyamba kubadwa, koma atagona ndi mkazi wamngʼono wa abambo ake, ulemu wake wokhala mwana woyamba unaperekedwa kwa ana a Yosefe. Kotero iye sanalembedwe pa mndandanda wa mayina ngati mwana woyamba kubadwa, ndipo ngakhalenso Yuda anali wamphamvu kwambiri pakati pa abale ake, ndi kuti wolamulira anachokera mwa iye, ulemu wa mwana woyamba kubadwa unaperekedwa kwa Yosefe) ana a Rubeni mwana woyamba wa Israeli ndi awa: Hanoki, Palu, Hezironi, ndi Karimi. Ana a Yoweli anali awa: Semaya, Gogi, Simei, Mika, Reaya, Baala, ndiponso Beeri, amene Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri anamugwira ukapolo. Mtsogoleri wa fuko la Rubeni anali Beeri. Abale awo mwa mabanja awo, potsata mndandanda wa mʼbado wawo, ndi awa: Yeiyeli, mtsogoleri, Zekariya, ndiponso Bela mwana wa Azazi, mwana wa Sema, mwana wa Yoweli. Iwo ankakhala ku Aroeri mpaka ku Nebo ndi Baala-Meoni. Iwo anakhala cha kummawa mpaka kukafika polowera mʼchipululu cha mbali ina ya Mtsinje wa Yufurate, chifukwa ziweto zawo zinaswana kwambiri mʼdziko la Giliyadi. Pa nthawi ya Sauli anachita nkhondo ndi Ahagiri ndi kuwagonjetsa. Tsono iwo anakhala mʼmatenti a Ahagiri ku dera lonse la kummawa kwa Giliyadi. Fuko la Gadi Anthu a fuko la Gadi anakhala moyandikana ndi fuko la Rubeni ku Basani mpaka ku Saleka: Mtsogoleri wawo ku Basani anali Yoweli, wachiwiri anali Safamu, kenaka Yanayi ndi Safati. Abale awo mwa mabanja awo anali awa: Mikayeli, Mesulamu, Seba, Yorayi, Yakani, Ziya ndi Eberi, onse ali asanu ndi awiri. Amenewa ndiwo anali ana a Abihaili, mwana wa Huri, mwana wa Yarowa, mwana wa Giliyadi, mwana wa Mikayeli, mwana wa Yesisayi, mwana wa Yahido, mwana wa Buzi. Ahi mwana wa Abdieli, mwana wa Guni, anali mtsogoleri wa banja la makolo awo. Fuko la Gadi linakhala ku Giliyadi, ku Basani ndi midzi yozugulira, madera onse a msipu a ku Saroni mpaka kumene amalekezera. Mayina onsewa analembedwa potsata mndandanda wa mibado yawo pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu mfumu ya Yuda ndi Yeroboamu mfumu ya Israeli. Mafuko a Rubeni, Gadi ndi theka la Manase, anali ndi anthu 44, 760 okonzeka kulowa usilikali; anthu amatupi amphamvu, amene amatha kugwiritsa ntchito chishango ndi lupanga, amene amatha kugwiritsa ntchito uta, amene anaphunzitsidwa kumenya nkhondo. Iwo anachita nkhondo ndi Ahagiri, Yeturi, Nafisi ndi Nodabu. Iwowo anathandizidwa polimbana nawo ndipo Mulungu anapereka Ahagiri mʼmanja mwawo; popeza iwo anafuwulira kwa Mulungu pa nkhondopo. Iye anayankha mapemphero awo chifukwa anamudalira. Choncho iwo analanda ziweto za Ahagiri: ngamira 50,000, nkhosa ndi mbuzi 250,000 ndi abulu 2,000. Ndiponso anagwira akapolo 100,000, enanso ambiri anaphedwa, chifukwa nkhondoyo inali ya Mulungu. Ndipo iwo anakhala mʼdzikomo mpaka pa nthawi ya ukapolo. Theka la Fuko la Manase Theka la fuko la Manase linkakhala ku dziko la kummawa kuyambira ku Basani mpaka ku Baala-Herimoni, kumene ndi ku Seniri (Phiri la Herimoni) ndipo anthuwo anali ochuluka kwambiri. Atsogoleri a mabanja awo anali awa: Eferi, Isi, Elieli, Azirieli, Yeremiya, Hodaviya ndi Yahidieli. Iwo anali asilikali olimba mtima, anthu otchuka, ndiponso atsogoleri a mabanja awo. Koma iwo anali osakhulupirika kwa Mulungu wa makolo awo ndipo anadzipereka okha kwa milungu ya anthu okhala mʼdzikomo amene Mulungu anawawononga pamene iwowo ankafika. Kotero Mulungu wa Israeli anayika mkwiyo mwa Puli mfumu ya Asuri (ameneyu ndi Tigilati-Pileseri mfumu ya Asuri) amene anatenga fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase kupita nawo ku ukapolo. Iye anapita nawo ku Hala, Habori, Hara ndi ku mtsinje wa Gozani, kumene ali mpaka lero lino. Fuko la Levi Ana a Levi anali awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Ana a Amramu anali awa: Aaroni, Mose ndi Miriamu. Ana a Aaroni anali awa: Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara Eliezara anabereka Finehasi, Finehasi anabereka Abisuwa, Abisuwa anabereka Buki, Buki anabereka Uzi. Uzi anabereka Zerahiya, Zerahiya anabereka Merayoti, Merayoti anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi. Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Ahimaazi. Ahimaazi anabereka Azariya, Azariya anabereka Yohanani, Yohanani anabereka Azariya (uyu ndi amene anatumikira monga wansembe mʼNyumba ya Mulungu imene Solomoni anamanga mu Yerusalemu), Azariya anabereka Amariya, Amariya anabereka Ahitubi, Ahitubi anabereka Zadoki, Zadoki anabereka Salumu, Salumu anabereka Hilikiya, Hilikiya anabereka Azariya, Azariya anabereka Seraya, ndipo Seraya anabereka Yehozadaki. Yehozadaki anagwidwa ukapolo pamene Yehova analola Nebukadinezara kuti agwire ukapolo Yuda ndi Yerusalemu. Ana a Levi anali awa: Geresomu, Kohati ndi Merari. Mayina a ana a Geresomu ndi awa: Libini ndi Simei. Ana a Kohati anali awa: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Ana a Merari anali awa: Mahili ndi Musi. Mayina a mabanja a fuko la Levi olembedwa potsata makolo awo ndi awa: Ana a Geresomu ndi awa: Libini, Yehati, Zima, Yowa, Ido, Zera ndi Yeaterai. Zidzukulu za Kohati ndi izi: Aminadabu, Kora, Asiri, Elikana, Ebiyasafu, Asiri, Tahati, Urieli, Uziya ndi Sauli. Zidzukulu za Elikana ndi izi: Amasai, Ahimoti, Elikana, Zofai, Nahati, Eliabu, Yerohamu, Elikana ndi Samueli. Ana a Samueli ndi awa: Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya. Zidzukulu za Merari ndi izi: Mahili, Libini, Simei, Uza, Simea, Hagiya ndi Asaya. Oyimba mʼNyumba ya Mulungu Awa ndi anthu amene Davide anawayika kuti aziyangʼanira mayimbidwe mʼNyumba ya Yehova, Bokosi la Chipangano litabwera kudzakhala mʼmenemo. Iwo ankatumikira akuyimba nyimbo pa khomo la malo opatulika, tenti ya msonkhano, mpaka Solomoni atamanga Nyumba ya Yehova mu Yerusalemu. Iwo ankagwira ntchito zawo potsata malamulo amene anawapatsa. Mayina a anthuwo, pamodzi ndi ana awo, anali awa: Ochokera ku banja la Kohati: Hemani, katswiri woyimba, anali mwana wa Yoweli, mwana wa Samueli, mwana wa Elikana, mwana wa Yerohamu, mwana wa Elieli, mwana wa Towa, mwana wa Zufi, mwana wa Elikana, mwana wa Mahati, mwana wa Amasai, mwana wa Elikana, mwana wa Yoweli, mwana wa Azariya, mwana wa Zefaniya, mwana wa Tahati, mwana wa Asiri, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, mwana wa Izihari, mwana wa Kohati, mwana wa Levi, mwana wa Israeli; ndi Asafu mʼbale wake, amene ankatumikira ku dzanja lake lamanja: Asafu anali mwana wa Berekiya, mwana wa Simea, mwana wa Mikayeli, mwana wa Baaseya, mwana wa Malikiya, mwana wa Etini, mwana wa Zera, mwana wa Adaya, mwana wa Etani, mwana wa Zima, mwana Simei, mwana wa Yahati, mwana wa Geresomu, mwana wa Levi; ndipo abale awo ena anali a banja la Merari amene amatumikira ku dzanja lake lamanzere: Etani anali mwana wa Kisi, mwana wa Abidi, mwana wa Maluki, mwana wa Hasabiya, mwana wa Amaziya, mwana wa Hilikiya, mwana wa Amizi, mwana wa Bani, mwana wa Semeri, mwana wa Mahili, mwana wa Musi, mwana wa Merari, mwana wa Levi. Abale awo Alevi anapatsidwa ntchito zina zonse ku malo opatulika ku nyumba ya Mulungu. Koma Aaroni ndi zidzukulu zake anali amene amapereka nsembe pa guwa lansembe zopsereza ndi pa guwa lansembe zofukiza pamodzi ndi zonse zimene zimachitika ku malo opatulika kwambiri, kuchita mwambo wopepesera Israeli, potsata zonse zimene Mose mtumiki wa Mulungu anawalamulira. Ana a Aaroni ndi zidzukulu zake anali awa: Eliezara, Finehasi, Abisuwa, Buki, Uzi, Zerahiya, Merayoti, Amariya, Ahitubi, Zadoki ndi Ahimaazi. Malo amene iwo anapatsidwa kuti likhale dziko lawo ndi awa: (Malowa anapatsidwa kwa zidzukulu za Aaroni zimene zinali za banja la Kohati, chifukwa malo oyamba kugawidwa anali awo). Iwo anapatsidwa Hebroni mʼdziko la Yuda ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. Koma minda ndi midzi yozungulira mzindawo zinapatsidwa kwa Kalebe mwana wa Yefune. Kotero zidzukulu za Aaroni zinapatsidwa Hebroni (mzinda wopulumukirako), ndi Libina, Yatiri, Esitemowa, Hileni, Debri, Asani, Yuta ndi Beti-Semesi pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. Ndipo ku fuko la Benjamini anapatsidwa Gibiyoni, Geba, Alemeti ndi Anatoti, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira malowa. Mizinda imene anapatsidwa ku banja la Kohati onse pamodzi inalipo 13. Zidzukulu zotsala za Kohati anazigawira midzi khumi kuchokera ku mabanja a fuko la theka la Manase. Zidzukulu za Geresomu banja ndi banja zinapatsidwa mizinda 13 kuchokera ku mafuko a Isakara, Aseri ndi Nafutali, ndi gawo lina la fuko la Manase limene lili ku Basani. Zidzukulu za Merari banja ndi banja zinapatsidwa mizinda khumi ndi iwiri kuchokera ku mafuko a Rubeni, Gadi ndi Zebuloni. Kotero Aisraeli anapatsa Alevi mizindayi ndi madera a msipu ozungulira malowa. Kuchokera ku mafuko a Yuda, Simeoni ndi Benjamini anawapatsa mizinda imene inawatchula kale mayina. Mabanja ena a Kohati anapatsidwanso malo kuchokera ku fuko la Efereimu. Kuchokera ku dziko lamapiri la Efereimu anapatsidwa Sekemu (mzinda wopulumukirako) ndi Gezeri, Yokineamu, Beti-Horoni, Ayaloni ndi Gati-Rimoni, pamodzi ndi madera odyetsera ziweto ozungulira. Ndipo kuchokera ku theka la fuko la Manase, Aisraeli anapereka Aneri ndi Bileamu pamodzi ndi madera odyetsera ziweto kwa mabanja ena onse a Kohati. Ageresomu analandira malo awa: Kuchokera ku theka la fuko la Manase, analandira Golani ku Basani ndiponso Asiteroti, ndi malo awo odyetsera ziweto; Kuchokera ku fuko la Isakara analandira Kedesi, Daberati, Ramoti ndi Anemu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto; kuchokera ku fuko la Aseri analandira Masala, Abidoni, Hukoki ndi Rehobu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto; ndipo kuchokera ku fuko la Nafutali analandira Kedesi ku Galileya, Hamoni ndi Kiriyataimu, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto. Amerari (Alevi ena onse) analandira madera awa: kuchokera ku fuko la Zebuloni, iwo analandira Yokineamu, Karita, Rimono ndi Tabori, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto; Kuchokera ku fuko la Rubeni kutsidya kwa Yorodani, kummawa kwa Yeriko, analandira Bezeri ku chipululu, Yaza, Kedemoti ndi Mefaati, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto; ndipo kuchokera ku fuko la Gadi analandira Ramoti ku Giliyadi, Mahanaimu, Hesiboni ndi Yazeri, pamodzi ndi malo ake odyetsera ziweto. Fuko la Isakara Ana a Isakara anali awa: Tola, Puwa, Yasubu ndi Simironi ndipo onse analipo anayi. Ana a Tola ndi awa: Uzi, Refaya, Yerieli, Yahimai, Ibisamu ndi Samueli. Awa anali atsogoleri a mabanja awo. Pa nthawi ya ulamuliro wa Davide zidzukulu za Tola zomwe zinali anthu odziwa kumenya nkhondo zinalipo 22,600. Mwana wa Uzi anali Izirahiya. Ana a Izirahiya anali: Mikayeli, Obadiya, Yoweli ndi Isiya. Onse asanu anali atsogoleri a mabanja. Monga mwa chiwerengero cha mabanja awo, panali anthu 36,000 odziwa kumenya nkhondo, pakuti iwo anali ndi akazi ndi ana ambiri. Abale awo onse a mʼbanja la Isakara amene anali odziwa kumenya nkhondo analipo 87,000, olembedwa potsata mibado yawo. Fuko la Benjamini Ana atatu a Benjamini anali awa: Bela, Bekeri ndi Yediaeli. Ana a Bela anali awa: Eziboni, Uzi, Uzieli, Yerimoti ndi Iri. Iwowa anali atsogoleri a mabanja awo ndipo onse pamodzi analipo asanu. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali anthu 22,034 odziwa kumenya nkhondo. Ana a Bekeri anali awa: Zemira, Yowasi, Eliezara, Eliyoenai, Omiri, Yeremoti, Abiya, Anatoti ndi Alemeti. Onsewa anali ana a Bekeri. Pa mndandanda wa mʼbado wawo panali atsogoleri a mabanja ndi anthu 20,200 odziwa kumenya nkhondo. Mwana wa Yediaeli anali Bilihani. Ana a Bilihani anali awa: Yeusi, Benjamini, Ehudi, Kenaana, Zetani, Tarisisi ndi Ahisahara. Ana onsewa a Yediaeli anali atsogoleri a mabanja. Analipo anthu 17,200 amene anali okonzeka kupita ku nkhondo. Asupi ndi Ahupi anali zidzukulu za Iri, ndipo Ahusimu anali zidzukulu za Aheri. Fuko la Nafutali Ana a Nafutali anali awa: Yahazieli, Guni, Yezeri ndi Salumu, zidzukulu za Biliha. Fuko la Manase Ana a Manase anali awa: Asirieli ndi mwana amene anabereka kwa mzikazi wake wa ku Aramu. Mzikazi yemweyo anaberekanso Makiri abambo ake a Giliyadi. Makiri anatenga mkazi wa banja la Ahupi ndi Asupi. Mlongo wake anali Maaka. Mwana wake wina anali Zelofehadi, amene anabereka ana aakazi okhaokha. Maaka mkazi wa Makiri anabereka mwana wamwamuna ndipo anamutcha Perezi. Mʼbale wake anamutcha Seresi, ndipo ana ake anali Ulamu ndi Rakemu. Mwana wa Ulamu anali Bedani. Awa anali ana a Giliyadi mwana wa Makiri, mwana wa Manase. Mlongo wake Hamoleketi anabereka Isihodi, Abiezeri ndi Mahila. Ana a Semida anali: Ahiyani, Sekemu, Likihi ndi Aniyamu. Fuko la Efereimu Ana a Efereimu anali awa: Sutela, Beredi, Tahati, Eliada, Tahati, Zabadi, Sutela. Ezeri ndi Eladi anaphedwa ndi anthu a ku Gati, pamene anabwera kudzalanda zoweta zawo. Efereimu, abambo awo, anawalira masiku ambiri, ndipo abale ake anabwera kudzamutonthoza. Kenaka anagona ndi mkazi wake, ndipo anakhala woyembekezera nabala mwana wamwamuna. Anamutcha dzina lake Beriya, chifukwa tsoka linagwera banja lake. Mwana wake wamkazi anali Seera, amene anamanga mzinda wa Beti-Horoni Wakumunsi, Wakumtunda kudzanso Uzeni-Seera. Mwana wina wa Efereimu anali Refa amene zidzukulu zake zinali Resefu, Tela, Tahani, Ladani, Amihudi, Elisama, Nuni ndi Yoswa. Malo amene ankakhala anali Beteli ndi midzi yozungulira, cha kummawa kunali Naarani, Gezeri ndi midzi yake ya kumadzulo ndi Sekemu ndi midzi yake mpaka ku Aya ndi midzi yake. Mʼmbali mwa malire a Manase munali Beti-Seani, Taanaki, Megido ndi Dori, pamodzi ndi midzi yake. Zidzukulu za Yosefe mwana wa Israeli zimakhala mʼmizinda imeneyi. Fuko la Aseri Ana a Aseri anali awa: Imuna, Isiva, Isivi ndi Beriya. Mlongo wawo anali Sera. Ana a Beriya anali awa: Heberi ndi Malikieli amene anabereka Birizaiti. Heberi anabereka Yafuleti, Someri, Hotamu ndi Suwa, mlongo wawo. Ana a Yafuleti anali awa: Pasaki, Bimuhali ndi Asivati. Awa anali ana a Yafuleti. Ana a Someri anali awa: Ahi, Rohiga, Yehuba ndi Aramu. Ana a mʼbale wake Helemu anali awa: Zofa, Imuna, Selesi ndi Amali. Ana a Zofa anali awa: Suwa, Harineferi, Suwali, Beri, Imula, Bezeri, Hodi, Sama, Silisa, Itirani ndi Bera. Ana a Yeteri anali awa: Yefune, Pisipa ndi Ara. Ana a Ula anali awa: Ara, Hanieli ndi Riziya. Onsewa anali zidzukulu za Aseri, atsogoleri a mabanja, anthu omveka, ankhondo olimba mtima, ndi akuluakulu pakati pa atsogoleri anzawo. Chiwerengero cha anthu odziwa kumenya nkhondo chomwe chinalembedwa chinali 26,000. Adzukulu a Benjamini ndi Sauli Benjamini anabereka Bela mwana wake woyamba, wachiwiri Asibeli, wachitatu Ahara, wachinayi Noha ndipo wachisanu Rafa. Ana a Bela anali awa: Adari, Gera, Abihudi, Abisuwa, Naamani, Ahowa, Gera, Sefufani ndi Hiramu. Zidzukulu za Ehudi, zimene zinali atsogoleri a mabanja a amene amakhala ku Geba ndipo zinasamutsidwa kupita ku Manahati zinali izi: Naamani, Ahiya ndi Gera, amene anawasamutsa ndipo anabereka Uza ndi Ahihudi. Saharaimu anabereka ana ku Mowabu atalekana ndi akazi ake, Husimu ndi Baara. Mwa mkazi wake Hodesi anabereka Yobabu, Zibiya, Mesa, Malikamu, Yeusi, Sakiya ndi Mirima. Awa ndiye ana ake, atsogoleri a mabanja awo. Mwa mkazi wake Husimu anabereka Abitubi ndi Elipaala. Ana a Elipaala anali awa: Eberi, Misamu, Semedi (amene anamanga mizinda ya Ono ndi Lodi ndi midzi yake yozungulira) ndiponso Beriya ndi Sema, amene anali atsogoleri a mabanja a amene ankakhala ku Ayaloni ndipo anathamangitsa nzika za ku Gati. Ahiyo, Sasaki, Yeremoti, Zebadiya, Aradi, Ederi, Mikayeli, Isipa ndi Yoha anali ana a Beriya. Zebadiya, Mesulamu, Hiziki, Heberi, Isimerai, Iziliya ndi Yobabu anali ana a Elipaala. Yakimu, Zikiri, Zabidi, Elienai, Ziletai, Elieli, Adaya, Beraya ndi Simirati anali ana a Simei. Isipani, Eberi, Elieli, Abidoni, Zikiri, Hanani, Hananiya, Elamu, Anitotiya, Ifideya ndi Penueli anali ana a Sasaki. Samuserai, Sehariya, Ataliya, Yaaresiya, Eliya ndi Zikiri anali ana a Yerohamu. Onsewa anali atsogoleri a mabanja, anthu otchuka potsata mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu. Yeiyeli amene amabereka Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni. Dzina la mkazi wake linali Maaka, ndipo mwana wake woyamba anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, Gedori, Ahiyo, Zekeri ndi Mikiloti, amene anabereka Simea. Iwowa ankakhalanso ku Yerusalemu ndi abale awo. Neri anabereka Kisi. Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala. Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika. Ana a Mika anali awa: Pitoni, Meleki, Tareya ndi Ahazi. Ahazi anabereka Yehoyada, Yehoyada anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimuri anabereka Moza. Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Rafa, Eleasa ndi Azeli. Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi, ndipo mayina awo anali awa: Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Onsewa anali ana a Azeli. Ana a Eseki mʼbale wake anali awa: Mwana wake woyamba Ulamu, wachiwiri Yeusi ndipo wachitatu Elifeleti. Ana a Ulamu anali asilikali olimba mtima amene amadziwa kugwiritsa ntchito uta. Iwo anali ndi ana ndi adzukulu ambiri ndipo onse analipo 150. Onsewa anali adzukulu a Benjamini. Aisraeli onse analembedwa potsata mibado yawo mʼbuku la mafumu a Aisraeli. Anthu a ku Yerusalemu Anthu a ku Yuda anatengedwa kunka ku ukapolo ku Babuloni chifukwa cha kusakhulupirika kwawo. Tsono anthu oyamba kukhala mʼmadera awo anali Aisraeli wamba, ansembe, Alevi ndi otumikira ku Nyumba ya Yehova. Anthu a ku Yuda, Benjamini ndi Efereimu ndiponso Manase amene anakhala mu Yerusalemu anali awa: Utai mwana wa Amihudi, mwana wa Omuri, mwana wa Imuri, mwana wa Bani, chidzukulu cha Perezi mwana wa Yuda. A banja la Siloni: Asaya mwana wake woyamba pamodzi ndi ana ake. A banja la Zera: Yeueli. Anthu ochokera ku Yuda analipo 690. A fuko la Benjamini: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Hodaviya, mwana wa Hasenuya; Ibineya mwana wa Yerohamu; Ela mwana wa Uzi, mwana wa Mikiri; ndi Mesulamu mwana wa Sefatiya, mwana wa Reueli mwana wa Ibiniya. Anthu ochokera ku Benjamini monga analembedwera mwa mibado yawo, analipo 956. Anthu onsewa anali atsogoleri a mabanja awo. Ansembe: Yedaya, Yehoyaribu; Yakini; Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki mwana wa Merayoti, mwana wa Ahitubi, wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Mulungu; Adaya mwana wa Yerohamu, mwana wa Pasi-Huri, mwana wa Malikiya; ndi Maasai mwana wa Adieli, mwana wa Yahizera, mwana wa Mesulamu, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri. Ansembe amene anali atsogoleri a mabanja awo analipo 1,760. Anali anthu amphamvu ndi odziwa kutumikira mʼnyumba ya Mulungu. Alevi: Semaya mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, wa mʼbanja la Merari; Bakibakara, Heresi, Galali ndi Mataniya mwana wa Mika, mwana wa Zikiri, mwana wa Asafu; Obadiya mwana wa Semaya mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni ndi Berekiya mwana wa Asa, mwana wa Elikana, amene ankakhala ku midzi ya Anetofati. Alonda a pa makomo: Salumu, Akubu, Talimoni, Ahimani ndi abale awo. Mtsogoleri wawo anali Salumu. Amenewa amakhala pa chipata cha mfumu kummawa mpaka lero lino. Alonda a gulu la Alevi anali awa: Salumu mwana wa Kore, mwana wa Ebiyasafu, mwana wa Kora, pamodzi ndi abale ake a ku banja la makolo ake, Akora aja ankanyangʼanira khomo la Tenti monga ankachitira abambo awo polondera khomo la malo okhalapo Yehova. Masiku oyamba Finehasi mwana wa Eliezara anali woyangʼanira alonda apakhomo ndipo Yehova anali naye. Zekariya mwana wa Meselemiya anali mlonda woyangʼanira pa chipata cha tenti ya msonkhano. Onse amene anasankhidwa kukhala alonda pa khonde analipo 212. Iwo analembedwa mwa mibado yawo ku midzi yawo. Davide ndi mneneri Samueli ndiwo anawayika mʼmalo awo antchito chifukwa cha kukhulupirika kwawo. Iwo ndi zidzukulu zawo anali oyangʼanira zipata za nyumba ya Yehova imene imatchedwa Tenti. Alonda apakhomowa anali mbali zonse zinayi: kummawa, kumadzulo, kumpoto ndi kummwera. Abale awo a ku midzi yawo amabwera nthawi ndi nthawi kudzagwira ntchito yawo kwa masiku asanu ndi awiri. Koma atsogoleri akuluakulu anayi a alonda, amene anali Alevi, anapatsidwa udindo woyangʼanira zipinda ndi chuma cha nyumba ya Mulungu. Iwo amakhala usiku wonse atayima mozungulira Nyumba ya Mulungu, chifukwa anayenera kuyilondera. Ndipo anali ndi kiyi wotsekulira mmawa uliwonse. Ena amayangʼanira zipangizo zimene amagwiritsa ntchito pa ntchito mʼNyumba ya Mulungu. Iwo amaziwerenga zikamalowetsedwa ndi potulutsidwa. Ena anapatsidwa udindo wosamalira zipangizo ndi zinthu zina zonse za ku malo opatulika, pamodzi ndi ufa, vinyo, mafuta, lubani ndi zonunkhira. Koma ansembe ena amasakaniza zonunkhirazo. Mlevi wotchedwa Matitiya mwana woyamba wa Salumu wa mʼbanja la Kora, anapatsidwa udindo woyangʼanira zophikidwa mʼziwaya. Abale ake ena a mʼbanja la Akohati amaphika buledi wa pa Sabata lililonse amene amayikidwa pa tebulo. Atsogoleri a mabanja a Alevi, amene anali ndi luso loyimba, amakhala mʼzipinda za Nyumba ya Mulungu ndipo samagwira ntchito zina chifukwa ankatumikira usana ndi usiku. Onsewa anali atsogoleri a mabanja a Alevi, akuluakulu monga analembedwera pa mibado yawo, ndipo ankakhala mu Yerusalemu. Mibado ya Sauli Yeiyeli abambo a Gibiyoni ankakhala ku Gibiyoni. Dzina la akazi awo linali Maaka, ndipo mwana wawo woyamba kubadwa anali Abidoni, motsatana ndi Zuri, Kisi, Baala, Neri, Nadabu, Gedori, Ahiyo, Zekariya ndi Mikiloti. Mikiloti anabereka Simeamu. Iwonso ankakhala ndi abale awo ku Yerusalemu. Neri anabereka Kisi, Kisi anabereka Sauli, ndipo Sauli anabereka Yonatani, Maliki-Suwa, Abinadabu ndi Esibaala. Mwana wa Yonatani anali Meri-Baala, amene anabereka Mika. Ana a Mika anali: Pitoni, Meleki, Tahireya ndi Ahazi. Ahazi anabereka Yara, Yara anabereka Alemeti, Azimaveti ndi Zimuri, ndipo Zimiri anabereka Moza. Moza anabereka Bineya. Ana ake anali Refaya, Eleasa ndi Azeli. Azeli anali ndi ana asanu ndi mmodzi ndipo mayina awo anali awa: Azirikamu, Bokeru, Ismaeli, Seariya, Obadiya ndi Hanani. Awa anali ana a Azeli. Sauli Adzipha Yekha Tsono Afilisti anachitanso nkhondo ndi Aisraeli ndipo Aisraeli anathawa Afilistiwo, kotero kuti ambiri anaphedwa pa phiri la Gilibowa. Afilisti anapanikiza kwambiri Sauli ndi ana ake, ndipo anapha Yonatani, Abinadabu ndi Maliki-Suwa. Nkhondo inakula kwambiri mozungulira Sauli ndipo pamene anthu amauta anamupeza, anamuvulaza. Tsono Sauli anawuza mnyamata wake wonyamula zida zake kuti, “Solola lupanga lako undiphe, kuopa kuti anthu osachita mdulidwewa angabwere ndi kudzandizunza ine.” Koma mnyamata wonyamula zida uja anachita mantha kwambiri ndipo sanathe kutero. Choncho Sauli anatenga lupanga lake lomwe nagwerapo. Mnyamata wonyamula zida zake uja ataona kuti Sauli wafa, nayenso anadzigwetsera pa lupanga lake nafa. Motero Sauli ndi ana ake atatu anafa, pamodzi ndi banja lake lonse anafera limodzi. Pamene Aisraeli onse amene anali mʼchigwa anaona kuti gulu lankhondo lathawa komanso kuti Sauli ndi ana ake aphedwa, nawonso anathawa kusiya mizinda yawo. Ndipo Afilisti anabwera kudzakhalamo. Mmawa mwake, Afilisti atabwera kudzatenga zinthu za anthu ophedwa, anapeza Sauli ndi ana ake atafa pa phiri la Gilibowa. Iwo anamuvula zovala zake, natenga mutu wake ndi zida zake zankhondo. Ndipo anatumiza amithenga mʼdziko lonse la Afilisti kukafalitsa nkhani yabwinoyi kwa mafano awo ndi kwa anthu awo. Iwo anayika zida zake zankhondo mʼnyumba zopembedzera milungu yawo ndipo anapachika mutu wake mʼnyumba ya Dagoni. Pamene anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi anamva zimene Afilisti anachitira Sauli, anthu awo onse olimba mtima anapita kukatenga mitembo ya Sauli ndi ana ake ndipo anabwera nayo ku Yabesi. Anakwirira mafupa awo pansi pa mtengo wabwemba ku Yabesi, ndipo anasala kudya masiku asanu ndi awiri. Sauli anafa chifukwa anali wosakhulupirika pamaso pa Yehova. Iye sanasunge mawu a Yehova, pakuti anakafunsira nzeru kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, sanafunsire nzeruzo kwa Yehova. Choncho Yehova anamupha ndi kupereka ufumu kwa Davide mwana wa Yese. Davide Adzozedwa Kukhala Mfumu ya Israeli Aisraeli onse anasonkhana pamaso pa Davide ku Hebroni ndipo anati, “Ife ndife abale anu. Kale lija, ngakhale pamene Sauli anali mfumu, inu ndinu amene munkatsogolera Aisraeli pa nkhondo zawo. Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwuzani kuti, ‘Iwe udzaweta anthu anga Aisraeli, ndipo udzakhala mfumu yawo.’ ” Akuluakulu onse a Israeli atafika kwa Mfumu Davide ku Hebroni, iye anachita nawo pangano pamaso pa Yehova, ndipo anamudzoza Davide kukhala mfumu ya Israeli, monga momwe Yehova analonjezera kudzera mwa Samueli. Davide Agonjetsa Yerusalemu Davide ndi Aisraeli onse anapita ku Yerusalemu (ku Yebusi). Ayebusi amene ankakhala kumeneko anamuwuza Davide kuti, “Simulowa muno.” Komabe Davide analanda linga la Ziyoni, limene ndi mzinda wa Davide. Davide anali atanena kuti “Aliyense amene adzatsogolere kukathira nkhondo Ayebusi adzakhala mkulu wa asilikali.” Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anayamba kupita, motero anakhala mkulu wa asilikali. Tsono Davide anakhazikika mu lingamo, ndipo mzindawu anawutcha Mzinda wa Davide. Iye anamanga malo onse ozungulira, kuyambira ku matsitso ozungulira khoma. Ndipo Yowabu anakonzanso mbali ina ya mzindawu. Ndipo mphamvu za Davide zinkakulirakulira chifukwa anali ndi Yehova Wamphamvuzonse. Asilikali Otchuka a Davide Awa ndiye anali atsogoleri amphamvu a Davide. Iwo pamodzi ndi Aisraeli onse, anathandiza kulimbikitsa ufumu wake kuti ukwanire madera onse, monga momwe Yehova analonjezera. Nawa mayina a ankhondo amphamvu a Davide: Yasobeamu Mhakimoni anali mkulu wa atsogoleri. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300 nthawi imodzi. Wotsatana naye anali Eliezara mwana wa Dodo Mwahohi, mmodzi mwa ankhondo atatu amphamvu. Iye anali ndi Davide ku Pasi-Damimu pamene Afilisti anasonkhana kudzachita nkhondo. Ankhondo anathawa Afilistiwo pamalo pamene panali munda wodzaza ndi barele. Koma awiriwo anayima pakati pa mundawo. Iwo anawuteteza, nakantha Afilistiwo ndipo Yehova anawapambanitsa koposa. Atatu mwa atsogoleri makumi atatu aja anabwera kwa Davide ku thanthwe ku phanga la Adulamu pamene gulu la Afilisti linali litamanga misasa mʼchigwa cha Refaimu. Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. Davide analakalaka madzi ndipo anati, “Haa, pakanapezeka munthu wokanditungira madzi a mʼchitsime chomwe chili pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu!” Choncho anthu atatuwa anadutsa mizere ya Afilisti, natunga madzi amene anali mʼchitsime chomwe chinali pafupi ndi chipata cha ku Betelehemu nabwera nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa. Mʼmalo mwake anathira pansi pamaso pa Yehova. Iye anati, “Inu Mulungu, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi ndimwe magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Chifukwa iwo anayika miyoyo yawo pachiswe kuti abweretse madziwo, Davide sanamwe. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo. Abisai mʼbale wa Yowabu ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300. Choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja. Iye analandira ulemu woposa atatuwo. Kotero anakhala mtsogoleri wawo ngakhale kuti iyeyo sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Benaya mwana wa Yehoyada wa ku Kabizeeli anali munthu wolimba mtima amene anachita zinthu zamphamvu. Iye anakantha ankhondo awiri otchuka a ku Mowabu. Tsiku lina kukuzizira kwambiri, iye analowa mʼdzenje ndi kuphamo mkango. Ndipo iye anakanthanso Mwigupto amene anali wotalika mamita awiri ndi theka. Ngakhale kuti Mwiguptoyo anali ndi mkondo wofanana ndi ndodo yowombera nsalu mʼdzanja mwake, Benaya anapita kukamenyana naye ali ndi chibonga chokha mʼmanja. Iye analanda mkondo mʼdzanja la Mwiguptoyo ndi kumupha ndi mkondo wake womwe. Izi ndi zamphamvu zimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iyeyo analinso wotchuka ngati anthu atatu amphamvu aja. Iye ankalemekezedwa kuposa wina aliyense mwa anthu makumi atatu, koma sanali mʼgulu la anthu atatu aja. Ndipo Davide anamuyika kukhala woyangʼanira asilikali omuteteza. Ankhondo amphamvuwa anali: Asaheli mʼbale wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu, Samoti Mharori, Helezi Mpeloni. Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abiezeri wa ku Anatoti, Sibekai Mhusati, Ilai Mwahohi, Maharai Mnetofa, Heledi mwana wa Baana Mnetofa, Itai mwana wa Ribai wa ku Gibeya ku Benjamini, Benaya Mpiratoni, Hurai wa ku zigwa za Gaasi, Abieli Mwaribati, Azimaveti Mbaharumi, Eliyahiba Msaaliboni, ana a Hasemu Mgizoni, Yonatani mwana wa Sage Mharari, Ahiamu mwana wa Sakari Mharari, Elifali mwana wa Uri, Heferi Mmekerati, Ahiya Mpeloni, Heziro wa ku Karimeli Naara mwana wa Ezibai, Yoweli mʼbale wa Natani, Mibihari mwana wa Hagiri, Zeleki Mwamoni, Naharai wa ku Beeroti, mnyamata wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya. Ira Mwitiri, Garebu Mwitiri, Uriya Mhiti, Zabadi mwana wa Ahilai, Adina mwana wa Siza Mrubeni, amene anali mtsogoleri wa Arubeni ndi anthu makumi atatu pamodzi naye, Hanani mwana wa Maaka, Yehosafati Mmitini, Uziya Mwasiterati, Sama ndi Yeiyeli ana a Hotamu Mwaroeri, Yediaeli mwana wa Simiri, ndi Yoha Mtizi mʼbale wake, Elieli Mhavati, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima Mmowabu, Elieli, Obedi ndi Yaasieli Mmeobai. Ankhondo Amene Anali ndi Davide, Sauli Asanafe Nawa anthu amene anabwera kwa Davide ali ku Zikilagi pamene iye anathamangitsidwa ndi Sauli mwana wa Kisi (iwowo anali mʼgulu la asilikali amene ankamuthandiza pa nkhondo. Iwo anali ndi mauta ndipo amadziwa kuponya mivi komanso miyala, ndipo amatha kuponyera dzanja lamanja kapena lamanzere. Iwo anali abale ake a Sauli ochokera ku fuko la Benjamini. Mtsogoleri wawo anali Ahiyezeri ndi Yowasi ana a Semaya wa ku Gibeya; Yezieli ndi Peleti ana a Azimaveti; Beraka, Yehu wa ku Anatoti, ndi Isimaiya wa ku Gibiyoni, munthu wamphamvu mʼgulu la anthu makumi atatu aja, yemwenso anali mtsogoleri wawo; Yeremiya, Yahazieli, Yohanani, Yozabadi wa ku Gederi, Eluzai, Yerimoti, Bealiya, Semariya ndi Sefatiya Mharufi; Elikana, Isiya, Azareli, Yowezeri ndi Yasobeamu a ku banja la Kora; ndi Yowela ndi Zebadiya ana a Yerohamu wa ku Gedori. Asilikali ena a fuko la Gadi anathawira kwa Davide ku linga lake ku chipululu. Iwo anali asilikali olimba mtima, okonzekera nkhondo ndipo amadziwa kugwiritsa ntchito chishango ndi mkondo. Iwowo anali woopsa ngati mikango ndipo anali aliwiro ngati ngoma zamʼmapiri. Mtsogoleri wawo anali Ezeri, wotsatana naye anali Obadiya, wachitatu anali Eliabu, wachinayi anali Misimana, Yeremiya anali wachisanu, wachisanu ndi chimodzi anali Atai, Elieli anali wachisanu ndi chiwiri, wachisanu ndi chitatu anali Yohanani, Elizabadi anali wachisanu ndi chinayi, wakhumi anali Yeremiya ndipo Makibanai anali wa 11. Anthu a fuko la Gadi amenewa anali atsogoleri; angʼonoangʼono amalamulira anthu 100 pamene akuluakulu amalamulira anthu 1,000. Awa ndi amene anawoloka Yorodani mwezi woyamba pamene mtsinje unali utasefukira mbali zonse, ndipo anathamangitsa aliyense amene amakhala mʼchigwa, mbali ya kumadzulo ndi kummawa. Anthu ena a fuko la Benjamini ndi ena ochokera ku Yuda anabweranso kwa Davide pamene anali ku linga lake. Davide anapita kukakumana nawo ndipo anati, “Ngati mwabwera kwa ine mwamtendere, kuti mundithandize, ndakonzeka kugwirizana nanu. Koma ngati mwabwera kudzandipereka kwa adani anga, ngakhale kuti sindinalakwe, Mulungu wa makolo anthu aone izi ndipo akuweruzeni.” Kenaka Mzimu anabwera pa Amasai, mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja ndipo anati: “Inu Davide, ife ndife anu! Tili nanu limodzi, inu mwana wa Yese! Kupambana, Kupambana kwa inu, ndiponso kupambana kukhale kwa iwo amene akukuthandizani pakuti Mulungu wanu adzakuthandizani.” Kotero Davide anawalandira ndipo anawayika kukhala atsogoleri a magulu ake a ankhondo. Anthu ena a fuko la Manase anathawira kwa Davide pamene anapita ndi Afilisti kukamenyana ndi Sauli. (Iye ndi anthu ake sanathandize Afilisti chifukwa, atsogoleri awo atakambirana, anamubweza Davide. Iwo anati, “Ife tidzawonongedwa ngati uyu adzabwerera kwa mbuye wake Sauli).” Davide atapita ku Zikilagi, anthu a fuko la Manase amene anathawira kwa iye anali awa: Adina, Yozabadi, Yediaeli, Mikayeli, Yozabadi, Elihu ndi Ziletai; atsogoleri a magulu a anthu 1,000 a ku Manase. Iwowa anathandiza Davide kulimbana ndi magulu achifwamba, pakuti onsewa anali asilikali olimba mtima ndipo anali atsogoleri mʼgulu lake la ankhondo. Tsiku ndi tsiku anthu amabwera kudzathandiza Davide, mpaka anakhala ndi gulu lalikulu la ankhondo, ngati gulu la ankhondo a Mulungu. Enanso Abwera kwa Davide ku Hebroni Nachi chiwerengero cha magulu a anthu ankhondo amene anabwera kwa Davide ku Hebroni kudzapereka ufumu wa Sauli kwa iye, monga momwe ananenera Yehova: Anthu a fuko la Yuda onyamula chishango ndi mkondo analipo 6,800; Anthu a fuko la Simeoni, asilikali okonzekera nkhondo analipo 7,100; Anthu a fuko la Levi analipo 4,600, mtsogoleri Yehoyada wa banja la Aaroni anabweranso ndi anthu 3,700, ndi Zadoki, mnyamata wankhondo wolimba mtima, anabwera ndi akuluakulu 22 ochokera mʼbanja lake; Anthu a fuko la Benjamini, abale ake a Sauli analipo 3,000 ndipo ambiri anali ndi Sauli ku nyumba yake pa nthawiyi; Anthu a fuko la Efereimu, asilikali olimba mtima, otchuka pa mabanja awo analipo 20,800; Anthu a fuko latheka la Manase amene anawayitana kuti adzakhazikitse nawo ufumu wa Davide analipo 18,000; Anthu a fuko la Isakara amene ankazindikira nthawi ndipo amadziwa zimene Israeli ankayenera kuchita, analipo atsogoleri 200 pamodzi ndi abale awo onse amene amawatsogolera. Anthu a fuko la Zebuloni, analipo 5,000. Iwowa anali asilikali odziwa bwino nkhondo, okhala ndi zida za mtundu uliwonse, okonzekera kudzathandiza Davide ndi mtima umodzi. Anthu a fuko la Nafutali, analipo atsogoleri 1,000 pamodzi ndi anthu 37,000 onyamula zishango ndi mikondo; Anthu a fuko la Dani, okonzekera nkhondo analipo 28,600. Anthu a fuko la Aseri, asilikali odziwa bwino nkhondo, okonzekeradi nkhondo analipo 40,000; Ndipo kuchokera kummawa kwa Yorodani, anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase, amene anali ndi zida za mtundu uliwonse analipo 120,000. Onsewa anali anthu odziwa kumenya nkhondo amene anadzipereka ku magulu awo. Iwo anabwera ku Hebroni ali otsimikiza kudzamuyika Davide kukhala mfumu ya Aisraeli. Aisraeli ena onse anali ndi mtima umodzinso womuyika Davide kukhala mfumu. Anthuwa anakhala ndi Davide masiku atatu akudya ndi kumwa pakuti mabanja awo anawapatsa zakudya. Komanso anthu oyandikana nawo ochokera ku Isakara, Zebuloni ndi Nafutali anabweretsa zakudya pa abulu, ngamira, nyulu ndi ngʼombe. Panali ufa wambiri, makeke ankhuyu, ntchintchi za mphesa, vinyo, mafuta, ngʼombe, nkhosa ndi mbuzi, popeza munali chimwemwe mu Israeli. Abweretsanso Bokosi la Chipangano Davide anakambirana ndi akuluakulu ake, atsogoleri a anthu 1,000 ndi atsogoleri a anthu 100. Ndipo anati kwa gulu lonse la Israeli, “Ngati kukukomerani komanso ngati chili chifuniro cha Yehova Mulungu wathu, tiyeni titumize uthenga kulikonse kumene kuli abale athu ena onse ku dziko lonse la Israeli ndiponso kwa ansembe ndi Alevi amene ali nawo mʼmidzi yawo ndi madera odyetsera ziweto, kuti abwere adzakhale nafe. Tiyeni tibweretsenso Bokosi la Mulungu wathu kuno kwathu, pakuti nthawi ya Sauli sitinafunse za bokosili.” Gulu lonse linavomereza izi, pakuti anthu onse anaona kuti kunali kofunika kutero. Kotero Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse, kuchokera ku mtsinje wa Sihori ku Igupto mpaka ku Lebo Hamati, kuti abweretse Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriati-Yearimu. Davide pamodzi ndi Aisraeli onse anapita ku Baalahi (Kiriati-Yearimu) ku Yuda kukatenga Bokosi la Yehova Mulungu, amene amakhala pakati pa akerubi. Limeneli ndiye Bokosi la Chipangano lomwe limadziwika ndi Dzina lake. Iwo anachotsa Bokosi la Mulungu ku nyumba ya Abinadabu pa ngolo yatsopano. Uza ndi Ahiyo ndiwo ankayendetsa ngoloyo. Davide pamodzi ndi Aisraeli onse ankakondwerera ndi mphamvu zawo zonse pamaso pa Mulungu, poyimba nyimbo pogwiritsa ntchito azeze, apangwe, matambolini, maseche ndi malipenga. Atafika pa malo opunthira tirigu ku Kidoni, Uza anatambalitsa dzanja lake kuti agwire bokosilo, chifukwa ngʼombe zinkafuna kugwa. Yehova anapsera mtima Uza ndipo anamukantha chifukwa chogwira bokosilo. Choncho iyeyo anafera pomwepo pamaso pa Mulungu. Ndipo Davide anakhumudwa chifukwa Yehova anakantha Uza ndipo mpaka lero malowo amatchedwa Perezi Uza. Tsiku limenelo Davide anachita mantha ndi Mulungu ndipo anafunsa kuti, “Kodi Bokosi la Mulungu lingafike bwanji kwathu?” Iye sanapitenso nalo Bokosi la Mulungu ku Mzinda wa Davide. Mʼmalo mwake anapita nalo ku nyumba ya Obedi-Edomu Mgiti. Ndipo Bokosi la Mulungu linakhala mʼbanja la Obedi-Edomu mʼnyumba mwake kwa miyezi itatu ndipo Yehova anadalitsa nyumba yake ndi chilichonse chimene anali nacho. Nyumba ya Davide ndi Banja Lake Hiramu mfumu ya ku Turo inatumiza amithenga kwa Davide pamodzi ndi mitengo ya mkungudza ndiponso amisiri a miyala ndi amisiri a matabwa kuti adzamumangire nyumba yaufumu. Choncho Davide anazindikira kuti Yehova wamukhazikitsa kukhala mfumu ya Israeli ndipo wakuza kwambiri ufumu wake chifukwa cha anthu ake, Aisraeli. Davide anakwatira akazi ena ambiri ku Yerusalemu ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi ambiri. Mayina a ana amene anaberekera ku Yerusalemu anali awa: Samua, Sobabu, Natani, Solomoni, Ibihari, Elisua, Elipeleti, Noga, Nefegi, Yafiya, Elisama, Beeliada ndi Elifeleti. Davide Agonjetsa Afilisti Afilisti atamva kuti Davide wadzozedwa kukhala mfumu ya dziko lonse la Israeli, iwo anapita mwamphamvu kukamusakasaka. Koma Davide atamva zimenezi anapita kukakumana nawo. Ndipo Afilisti anabwera ndi kulanda zinthu mʼChigwa cha Refaimu. Davide anafunsa Mulungu kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Afilisti? Kodi mukawapereka mʼmanja mwanga?” Yehova anamuyankha kuti, “Pita, Ine ndidzawapereka mʼmanja mwako.” Choncho Davide ndi anthu ake anapita ku Baala-Perazimu ndi kugonjetsa Afilistiwo. Iye anati, “Monga amasefukira madzi, Mulungu waphwanya adani anga ine ndikuona.” Motero anawatcha malowa Baala Perazimu. Afilisti anasiya milungu yawo kumeneko ndipo Davide analamulira kuti itenthedwe ndi moto. Nthawi inanso Afilisti anadzalanda katundu mu Chigwamo. Choncho Davide anafunsa Mulungu ndipo Mulunguyo anayankha kuti, “Usapite molunjika, koma uzungulire kumbuyo kwawo. Ukawathire nkhondo patsogolo pa mitengo ya mkandankhuku. Mukakangomva phokoso pa msonga za mitengo ya mkandankhuku, mukapite kukamenyana nawo, chifukwa izi zikasonyeza kuti Mulungu ali patsogolo panu kukantha ankhondo a Afilisti.” Kotero Davide anachita zimene Mulungu anamulamulira ndipo anakantha ankhondo a Afilisti njira yonse kuchokera ku Gibiyoni mpaka ku Gezeri. Choncho mbiri ya Davide inafalikira dziko lonse, ndipo Yehova anachititsa kuti mayiko ena azimuopa. Bokosi la Chipangano Alibweretsa ku Yerusalemu Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti. Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.” Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse mu Yerusalemu kuti abweretse Bokosi la Yehova ku malo amene analikonzera. Iye anayitanitsa pamodzi zidzukulu za Aaroni ndi Alevi: kuchokera ku banja la Kohati, mtsogoleri Urieli ndi abale ake 120. Kuchokera ku banja la Merari, mtsogoleri Asaya ndi abale ake 220; kuchokera ku banja la Geresomu, mtsogoleri Yoweli ndi abale ake 130; kuchokera ku banja la Elizafani, mtsogoleri Semaya ndi abale ake 200; kuchokera ku banja la Hebroni, mtsogoleri Elieli ndi abale ake 80; kuchokera ku banja la Uzieli, mtsogoleri Aminadabu ndi abale ake 112. Kenaka Davide anayitanitsa ansembe Zadoki ndi Abiatara, ndi Alevi awa, Urieli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu. Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu atsogoleri a mabanja a Alevi ndipo inu ndi abale anu Alevi mudziyeretse nokha ndi kubweretsa Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli ku malo amene ine ndalikonzera. Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.” Kotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa ndi cholinga chakuti akatenge Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli. Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova. Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga. Kotero Alevi anasankha Hemani mwana wa Yoweli; ndipo mwa abale ake anasankha Asafu mwana wa Berekiya; ndipo mwa ana a Merari, abale awo, anasankha Etani mwana wa Kusaya; ndipo pamodzi ndi iwowa abale awo otsatana nawo: Zekariya, Yaazieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli, alonda a pa chipata. Anthu oyimba aja Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo ankayimba ziwaya za malipenga zamkuwa; Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Maaseya ndi Benaya ankayimba azeze a liwu lokwera; ndipo Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu, Yeiyeli ndi Azaziya ankayimba apangwe a liwu lotsika. Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi anali woyangʼanira mayimbidwe; uwu ndiye unali udindo wake pakuti anali waluso pa zimenezi. Berekiya ndi Elikana anali olondera pa khomo la bokosilo. Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo. Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera. Popeza Mulungu anathandiza Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, anapereka nsembe ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndiponso nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri. Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala. Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe. Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake. Iwo anabwera nalo Bokosi la Mulungu ndipo analiyika pamalo pake mʼkati mwa tenti imene Davide anayimika ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano pamaso pa Mulungu. Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova. Kenaka anagawira Mwisraeli aliyense, wamwamuna ndi wamkazi, aliyense buledi mmodzi, nthuli yanyama ndiponso keke yamphesa zowuma. Iye anasankha Alevi ena kuti azitumikira pamene panali Bokosi la Yehova, kuti azipemphera, azithokoza ndi kulemekeza Yehova Mulungu wa Israeli. Mtsogoleri wawo anali Asafu, wachiwiri anali Zekariya, kenaka Yeiyeli, Semiramoti, Yehieli, Matitiya, Eliabu, Benaya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli. Iwo amayimba azeze ndi apangwe, Asafu amayimba ziwaya za malipenga, ndipo ansembe Benaya ndi Yahazieli amawomba malipenga nthawi zonse pamaso pa Bokosi la Chipangano la Mulungu. Nyimbo Yotamanda ya Davide Tsiku limeneli Davide anayamba nʼkusankha Asafu ndi anzake kuti ndiwo apereke nyimbo iyi ya matamando kwa Yehova: Yamikani Yehova, itanani dzina lake; lalikani za ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu. Imbirani Iye, muyimbireni nyimbo zamatamando; nenani za ntchito zake zonse zodabwitsa. Nyadirani dzina lake loyera; ikondwere mitima ya iwo akufunafuna Yehova. Dalirani Yehova ndi mphamvu zake; funafunani nkhope yake nthawi zonse. Kumbukirani ntchito zodabwitsa wazichita, zozizwitsa zake, ndi kuweruza kwa mʼkamwa mwake, inu zidzukulu za Israeli mtumiki wake, inu ana a Yakobo, osankhidwa ake. Iye ndiye Yehova Mulungu wathu; chiweruzo chake chili pa dziko lonse lapansi. Iye amakumbukira pangano lake nthawi zonse, mawu amene Iye analamula, kwa mibado miyandamiyanda, pangano limene anachita ndi Abrahamu, lonjezo limene analumbira kwa Isake. Iye analitsimikiza kwa Yakobo monga lamulo, kwa Israeli monga pangano lamuyaya. “Kwa iwe, ine ndidzapereka dziko la Kanaani monga cholowa chimene udzachilandira.” Ali anthu owerengeka, ochepa ndithu, komanso alendo mʼdzikomo, iwo anayendayenda kuchoka ku mtundu wina kupita ku mtundu wina, ku ufumu wina kupita ku ufumu wina. Iye sanalole munthu aliyense kuti awapondereze; chifukwa cha iwo, Iye anadzudzula mafumu: “Musakhudze odzozedwa anga; musawachitire choyipa aneneri anga.” Imbirani Yehova, dziko lonse lapansi; lalikani za chipulumutso chake tsiku ndi tsiku. Lengezani za ulemerero wake kwa mitundu yonse, ntchito zake zonse zodabwitsa kwa anthu onse. Pakuti Yehova ndi wamkulu ndi woyenera kwambiri kumutamanda; Iyeyo ayenera kuopedwa kuposa milungu yonse. Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano wopanda pake, koma Yehova analenga kumwamba. Ulemerero ndi ufumu zili pamaso pake; mphamvu ndi chimwemwe zili pa malo pokhala Iye. Perekani kwa Yehova, Inu mabanja a anthu a mitundu ina, perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu, perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake. Bweretsani chopereka ndipo mufike pamaso pake; pembedzani Yehova mu ulemerero wachiyero chake. Njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi! Dziko linakhazikika kolimba; silingasunthidwe. Zakumwamba zisangalale, dziko lapansi likondwere; anene anthu a mitundu ina, “Yehova ndi mfumu!” Nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo; minda ikondwere, ndi zonse zili mʼmenemo! Ndipo mitengo ya mʼnkhalango idzayimba, idzayimba chifukwa cha chimwemwe pamaso pa Yehova, pakuti akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Yamikani Yehova, pakuti Iye ndi wabwino; chikondi chake chikhala mpaka muyaya. Fuwulani kuti, “Tipulumutseni, Inu Mulungu wa chipulumutso chathu, mutisonkhanitse ndipo mutipulumutse kwa anthu a mitundu ina, kuti tiyamike dzina lanu loyera, kuti tikutamandeni.” Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli, kuyambira muyaya mpaka muyaya. Ndipo anthu onse anati, “Ameni” ndipo “Tikutamandani Yehova.” Ndipo Davide anasiya Asafu pamodzi ndi anzake kumene kunali Bokosi la Chipangano la Yehova kuti azitumikira kumeneko nthawi zonse, monga mwa zoyenera kuchita pa tsiku lililonse. Iye anasiyanso Obedi-Edomu pamodzi ndi anzake 68 kuti azitumikira nawo pamodzi. Obedi-Edomu mwana wa Yedutuni ndi Hosa anali alonda a pa chipata. Davide anasiya wansembe Zadoki ndi ansembe anzake ku chihema cha Yehova ku malo achipembedzo ku Gibiyoni kuti azipereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa guwa lansembe nthawi zonse mmawa ndi madzulo, potsata zonse zimene zinalembedwa mʼbuku la malamulo a Yehova, amene anawapereka kwa Aisraeli. Anthuwo anali pamodzi ndi Hemani ndi Yedutuni ndi onse amene anawasankha mowatchula dzina kuti apereke mayamiko kwa Yehova, “pakuti chikondi chake ndi chosatha.” Hemani ndi Yedutuni anali oyangʼanira malipenga ndi ziwaya ndiponso zipangizo zina zoyimbira nyimbo zachipembedzo. Ana a Yedutuni anawayika kuti aziyangʼanira pa chipata. Kenaka anthu onse anachoka, aliyense kupita kwawo. Ndipo Davide anabwerera ku nyumba kwake kukadalitsa banja lake. Lonjezo la Mulungu kwa Davide Davide atakhazikika mʼnyumba yake yaufumu, anawuza mneneri Natani kuti, “Ine pano ndikukhala mʼnyumba yaufumu yomanga ndi mitengo ya mkungudza, pomwe Bokosi la Chipangano la Yehova lili mu tenti.” Natani anayankha Davide kuti, “Chitani chilichonse chimene chili mu mtima mwanu, chifukwa Mulungu ali nanu.” Usiku umenewo mawu a Mulungu anafika kwa Natani, ndipo anati, “Pita kamuwuze mtumiki wanga Davide kuti, ‘Yehova akunena kuti, sudzandimangira ndiwe nyumba yokhalamo.’ Ine sindinakhalepo mʼnyumba kuyambira tsiku limene ndinatulutsa Israeli mʼdziko la Igupto mpaka lero lino. Ndakhala ndikuyenda kuchoka mʼtenti ina kupita mʼtenti ina, kuchoka malo ena kupita malo ena. Konse ndakhala ndikuyenda ndi Aisraeli onse, kodi ndinanenapo kwa wina aliyense wa atsogoleri awo amene ndinamulamula kuweta anthu anga kuti, ‘Kodi nʼchifukwa chiyani simunandimangire nyumba ya mitengo ya mkungudza?’ ” Ndipo tsopano umuwuze mtumiki wanga Davide kuti, “Yehova Wamphamvuzonse akuti, Ine ndinakutenga ku busa ukuweta nkhosa, kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga, Aisraeli. Ineyo ndinali nawe kulikonse kumene unkapita, ndipo ndachotsa adani ako onse pamaso pako. Tsopano ndidzakuza dzina lako kuti likhale mʼgulu la mayina a anthu otchuka kwambiri pa dziko lapansi. Ndipo ndidzawapatsa malo anthu anga, Aisraeli ndipo ndidzawadzala pamalo awoawo kuti asadzavutitsidwenso. Anthu oyipa sadzawazunzanso monga ankachitira poyamba paja; monga akhala akuchitira kuchokera nthawi imene ndinasankha atsogoleri a anthu anga Aisraeli. Ine ndidzagonjetsanso adani anu onse. “ ‘Ine ndikulengeza kwa iwe kuti Yehova adzakhazikitsa banja lako. Masiku ako akadzatha ndipo ukadzatsatira makolo ako, Ine ndidzawutsa mphukira yako imene idzalowa mʼmalo mwako, mmodzi mwa ana ako, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. Iye ndiye amene adzandimangira nyumba, ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya. Ine ndidzakhala abambo ake, ndipo iye adzakhala mwana wanga. Ine sindidzasiya kumukonda monga ndinachitira ndi amene unalowa mʼmalo mwawo. Ndidzamuyika kukhala wolamulira nyumba yanga ndi ufumu wanga kwamuyaya. Mpando wake waufumu udzakhazikika kwamuyaya.’ ” Natani anafotokozera Davide mawu onse avumbulutso limene analandira. Pemphero la Davide Choncho Mfumu Davide analowa mu tenti nakhala pamaso pa Yehova, ndipo anati, “Ine ndine yani, Inu Yehova Mulungu, ndipo banja langa nʼchiyani kuti mundifikitse pamene ndafikapa? Inu Mulungu, kukhala ngati izi ndi zosakwanira pamaso panu, Inuyo mwayankhula zatsogolo la banja la mtumiki wanu. Mwandiyangʼana ndipo mwandiyesa ngati munthu wolemekezeka kwambiri pakati pa anthu, Inu Yehova Mulungu.” “Kodi Davide anenenso chiyani kwa Inu, pakuti mwachitira ulemu wotere mtumiki wanu? Pakuti Inu mukumudziwa mtumiki wanu. Inu Yehova, chifukwa cha mtumiki wanu komanso mwa chifuniro chanu, mwachita chinthu chachikulu ichi ndipo mwawulula malonjezo anu aakulu onse. “Palibe wina wofanana nanu, Inu Yehova, ndipo palibe Mulungu wina koma Inu nokha monga tamvera ndi makutu athu. Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola, monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? Inu munawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo. “Ndipo tsopano Yehova, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake, likhazikitseni kwamuyaya. Chitani monga mwalonjezera, kotero dzina lanu likhazikike ndi kukhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa woyangʼanira Israeli, ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu. “Inu Mulungu wanga, mwaululira mtumiki wanu kuti mudzamumangira nyumba. Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. Inu Yehova, ndinu Mulungu! Mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. Ndipo chakukomerani kudalitsa banja la mtumiki wanu kuti likhale pamaso panu mpaka muyaya. Pakuti Inu Yehova mwalidalitsa, lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.” Nkhondo za Davide ndi Kupambana Kwake Patapita nthawi, Davide anagonjetsa Afilisti ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Iye analanda Gati ndi midzi yake yozungulira mʼmanja mwa Afilistiwo. Davide anagonjetsanso Amowabu, nakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho kwa iye. Komanso Davide anagonjetsa Hadadezeri mfumu ya Zoba, mpaka ku Hamati, pamene anapita kukakhazikitsa ulamuliro wake mʼmbali mwa mtsinje wa Yufurate. Davide analanda magaleta 1,000, anthu okwera magaleta 7,000 pamodzi ndi asilikali oyenda pansi 20,000. Iye anadula mitsempha ya akavalo onse okoka magaleta, koma anasiyapo akavalo 100 okha. Aramu wa ku Damasiko atabwera kudzathandiza Hadadezeri mfumu ya ku Zoba, Davide anakantha asilikali 22,000. Iye anakhazikitsa maboma mu ufumu wa Aramu wa ku Damasiko, ndipo Aaramu anakhala pansi pa ulamuliro wake ndipo ankapereka msonkho. Yehova ankamupatsa chipambano Davide kulikonse kumene ankapita. Davide anatenga zishango zagolide zimene ankanyamula akuluakulu ankhondo a Hadadezeri ndi kubwera nazo ku Yerusalemu. Kuchokera ku Teba ndi Kuni, mizinda ya Hadadezeri, Davide anatengako mkuwa wambiri umene Solomoni anapangira chimbiya, zipilala ndi zida zosiyanasiyana zamkuwa. Tou, mfumu ya Hamati atamva kuti Davide wagonjetsa gulu lonse lankhondo la Hadadezeri mfumu ya Zoba, anatumiza mwana wake Hadoramu kwa mfumu Davide kukamulonjera ndi kukamuyamikira chifukwa cha kupambana kwake pa nkhondo yake ndi Hadadezeriyo, amene analinso pa nkhondo ndi Tou. Hadoramu anabweretsa ziwiya zosiyanasiyana zagolide, zasiliva ndi zamkuwa. Mfumu Davide inapereka zinthu zimenezi kwa Yehova, monga anachitira ndi siliva ndi golide zochokera ku mayiko ena onse monga Edomu ndi Mowabu, Aamoni ndi Afilisti, ndi Aamaleki. Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu 18,000 mu Chigwa cha Mchere. Iye anayika maboma ku Edomu, ndipo Aedomu onse anakhala pansi pa Davide. Yehova ankapambanitsa Davide kulikonse kumene ankapita. Akuluakulu a Davide Davide analamulira dziko lonse la Israeli ndipo ankachita zonse mwachilungamo ndi molondola pamaso pa anthu ake onse. Yowabu, mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika; Zadoki, mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Savisa anali mlembi; Benaya mwana wa Yehoyada anali mtsogoleri wa Akereti ndi Apeleti, ndipo ana a Davide anali alangizi a mfumu. Davide Achita Nkhondo ndi Aamoni Patapita nthawi Nahasi mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake. Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni kudzamupepesa, atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi anthuwa sanawatumize kuti adzaone dziko lathu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anawameta ndi kudula zovala zawo pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera ndipo anawabweza kwawo. Munthu wina atafika ndi kufotokozera Davide za anthuwo, iye anatuma amithenga kukakumana nawo, chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.” Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, Hanuni ndi Aamoni anatumiza siliva wolemera makilogalamu 34,000 kuti akalipirire magaleta ndi okwerapo ake a ku Mesopotamiya; Aramu-Maaka ndi Zoba. Iwo analipira magaleta okwanira 32,000, pamodzi ndi mfumu ya ku Maaka ndi ankhondo ake. Amenewa anabwera ndi kudzamanga misasa yawo pafupi ndi Medeba. Nawonso Aamoni anabwera kuchokera ku mizinda yawo ndipo anapita kukachita nkhondo. Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene mafumu amene anabwera nawo anali kwa wokha, ku malo wopanda mitengo. Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake; iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse; koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.” Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai mʼbale wake ndi kulowa mu mzinda. Motero Yowabu anabwerera ku Yerusalemu. Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, pamodzi ndi mtsogoleri wa ankhondo wa Hadadezeri, Sofaki akuwatsogolera. Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani. Iyeyo anapita kukakumana nawo ndipo anakhala mʼmizere yankhondo moyangʼanana ndipo iwo anamenyana naye. Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 7,000 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Iye anaphanso Sofaki, mtsogoleri wawo wankhondo. Mafumu amene ali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anachita mtendere ndi Davide ndipo anakhala pansi pa ulamuliro wake. Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni. Davide Alanda Raba Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Yowabu anatsogolera gulu la ankhondo. Iye anawononga Aamoni, kenaka anapita ku mzinda wa Raba ndipo anawuzungulira, koma Davide anatsala ku Yerusalemu. Yowabu anathira nkhondo mzinda wa Raba ndipo anawuwononga. Davide anachotsa chipewa chaufumu pamutu pa mfumu yawo. Chipewacho chinkalemera makilogalamu asanu agolide ndiponso chinali ndi miyala yokongola. Ndipo Davide anavala chipewacho. Iye anatenga katundu wambiri kuchokera mu mzindawo, ndipo anatulutsa anthu amene anali mʼmenemo, nawayika kuti azigwira ntchito ya macheka, yosula makasu ndi nkhwangwa. Davide anachita izi ndi mizinda yonse ya Aamoni. Kenaka Davide pamodzi ndi gulu lake lonse lankhondo anabwerera ku Yerusalemu. Davide Achita Nkhondo ndi Afilisti Patapita nthawi, nkhondo inayambika pakati pa Aisraeli ndi Afilisti ku Gezeri. Nthawi imeneyo Sibekai Mhusati anapha Sipai, mmodzi mwa zidzukulu za Arefai, ndipo Afilisti anagonja. Pa nkhondo inanso ndi Afilisti, Elihanani mwana wa Yairi anapha Lahimi mʼbale wake wa Goliati Mgiti, amene mkondo wake unali ngati ndodo yowombera nsalu. Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati, panali munthu wina wamtali kwambiri, wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. Pamene iye ankanyoza Aisraeli, Yonatani mwana wa Simea, mʼbale wake wa Davide anamupha. Anthu amenewa anali zidzukulu za Rafa ku Gati, ndipo anaphedwa ndi Davide ndi ankhondo ake. Davide Awerenga Ankhondo Ake Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli. Choncho Davide anati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, “Pitani mukawerenge Aisraeli kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani. Ndipo mudzandiwuze kuti ndidziwe chiwerengero chawo.” Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?” Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu. Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda. Koma Yowabu sanaphatikizepo fuko la Levi ndi fuko la Benjamini pa chiwerengerochi, pakuti lamulo la mfumu linamuyipira. Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli. Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.” Yehova anati kwa Gadi, mlosi wa Davide, “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ” Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa Iye, “Yehova akuti, ‘Musankhepo chimene mungakonde kuti chichitike: mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.” Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.” Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000. Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba. Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.” Pamenepo mngelo wa Yehova analamula Gadi kuti awuze Davide kuti akamange guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. Ndipo Davide anapita pomvera mawu amene Gadi ananena mʼdzina la Yehova. Pamene Arauna ankapuntha tirigu, anatembenuka ndipo anaona mngelo ndipo ana ake anayi aamuna amene anali naye anabisala. Davide anayandikira, ndipo Arauna atayangʼana ndi kumuona, anachoka popunthira tirigupo ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi pamaso pa Davide. Davide anati kwa Arauna, “Undipatse malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe, kuti mliri uli pa anthuwa usiye. Undigulitse ine pa mtengo woyenera ndithu.” Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.” Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.” Choncho Davide analipira Arauna masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo. Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Iye anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anayankha potumiza moto pa guwa lansembe zopsereza kuchokera kumwamba. Tsono Yehova anayankhula kwa mngelo, ndipo analowetsa lupanga lake mʼchimake. Pa nthawi imeneyo, Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi, anapereka nsembe pamenepo. Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni. Koma Davide sanathe kupita kumeneko kuti akapemphere pamaso pa Yehova, chifukwa amaopa lupanga la mngelo wa Yehova. Ndipo Davide anati, “Nyumba ya Yehova Mulungu idzakhala pano, ndiponso guwa lansembe zopsereza za Israeli.” Kukonzekera Kumanga Nyumba ya Mulungu Choncho Davide analamula kuti asonkhanitse alendo onse amene amakhala mu Israeli ndipo kuchokera pakati pawo anasankha amisiri a miyala kuti aseme miyala yomangira nyumba ya Mulungu. Ndipo anapereka zitsulo zambiri zopangira misomali ya zitseko za pa zipata ndi zolumikiza zake. Anaperekanso mkuwa wochuluka wokanika kuwuyeza. Iye anaperekanso mitengo yambiri ya mkungudza, yosawerengeka, pakuti anthu a ku Sidoni ndi a ku Turo anabweretsa yambiri kwa Davide. Davide anati, “Mwana wanga Solomoni ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Koma nyumba yomwe timangire Yehova iyenera kukhala yaulemerero, yotchuka ndi yokongola pamaso pa anthu a mitundu yonse. Choncho ndikonzekeratu zambiri.” Motero Davide anayikonzekera kwambiri asanamwalire. Tsono iye anayitana Solomoni mwana wake ndipo anamulamula kuti adzamangire nyumba Yehova Mulungu wa Israeli. Davide anati kwa Solomoni, “Mwana wanga, ine ndinali ndi maganizo oti ndimangire nyumba Dzina la Yehova Mulungu wanga. Koma Yehova anandiyankhula kuti, ‘Iwe wapha anthu ambiri ndiponso wachita nkhondo zambiri. Sumangira dzina langa nyumba chifukwa wapha anthu ambiri pa dziko lapansi pamaso panga. Koma udzabala mwana wamwamuna amene adzakhala munthu wamtendere ndi wabata ndipo ndidzamupatsa mpumulo kuchokera kwa adani ake onse a mbali zonse. Dzina lake adzatchedwa Solomoni ndipo Ine ndidzapereka mtendere ndi bata kwa Israeli pa nthawi ya ulamuliro wake. Iye ndiye adzandimangire nyumba. Adzakhala mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ndipo ndidzakhazikitsa mpando wake waufumu mʼdziko la Israeli mpaka muyaya.’ ” “Tsopano mwana wanga, Yehova akhale nawe ndipo upambane ndi kumanga Nyumba ya Yehova Mulungu wako, monga momwe Iye ananenera kuti udzatero. Yehova akupatse nzeru ndi kumvetsetsa pamene Iye adzakuyika kukhala wolamulira Israeli, kuti udzasunge malamulo a Yehova Mulungu wako. Ndipo udzapambana ngati udzamvera mosamala malangizo ndi malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisraeli kudzera mwa Mose. Khala wamphamvu ndi wolimba mtima. Usachite mantha kapena kutaya mtima. “Ine movutikira kwambiri ndapereka ku Nyumba ya Mulungu matani 3,400 agolide, matani 34,000 asiliva, ndiponso mkuwa ndi chitsulo, matabwa ndi miyala. Ndipo iwe utha kuwonjezerapo pa zimenezi. Iwe uli ndi antchito ambiri: osema miyala, amisiri a miyala, ndi amisiri a matabwa, komanso anthu ambiri aluso la ntchito zosiyanasiyana, zagolide ndi zasiliva, zamkuwa, zazitsulo, amisiri osawerengeka. Tsopano yamba ntchito, ndipo Yehova akhale nawe.” Tsono Davide analamula atsogoleri onse a Israeli kuti athandize Solomoni mwana wake. Iye anawawuza kuti, “Kodi Yehova Mulungu, sali nanu? Ndipo Iye siwakupatsani mpumulo mbali zonse? Pakuti Iyeyo wapereka eni nthaka kwa inu ndipo dziko lili pa ulamuliro wa Yehova ndi anthu ake. Tsono perekani mtima wanu ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu. Yambani kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti mubweretse Bokosi la Chipangano la Yehova ndi zinthu zopatulika za Mulungu mʼNyumba ya Mulungu imene idzamangidwa chifukwa cha dzina la Yehova.” Fuko la Levi Davide atakalamba, ali ndi zaka zambiri, anayika Solomoni mwana wake kukhala mfumu ya Israeli. Iye anasonkhanitsanso pamodzi atsogoleri onse a Israeli, pamodzi ndi ansembe ndi Alevi. Anawerenga Alevi kuyambira a zaka makumi atatu ndi kupitirirapo, ndipo chiwerengero cha amuna onse chinali 38,000. Davide anati, “Mwa amenewa, amuna 24,000 aziyangʼanira ntchito za mʼNyumba ya Mulungu ndipo 6,000 akhale akuluakulu ndi oweruza. Amuna 4,000 akhale alonda a pa zipata ndipo 4,000 azitamanda Yehova ndi zipangizo zoyimbira zimene ndazipereka ndi cholinga chimenecho.” Davide anagawa Aleviwo mʼmagulumagulu motsatira ana a Levi awa: Geresoni, Kohati ndi Merari. Banja la Geresoni Ana a Geresoni: Ladani ndi Simei. Ana a Ladani: Mtsogoleri Yehieli, Zetamu ndi Yoweli. Onse analipo atatu. Ana a Simei: Selomoti, Haziyeli ndi Harani. Onse analipo atatu. Awa anali atsogoleri a mabanja a Ladani. Ndipo ana a Simei anali: Yahati, Zina, Yeusi ndi Beriya. Awa anali ana a Semei. Onse analipo anayi. Mtsogoleri anali Yahati, ndipo Ziza anali wachiwiri, koma Yeusi ndi Beriya analibe ana aamuna ambiri. Kotero iwo anawerengedwa ngati banja limodzi ndipo anapatsidwa ntchito imodzinso yofanana. Banja la Kohati Ana a Kohati: Amramu, Izihari, Hebroni ndi Uzieli. Onse analipo anayi. Ana a Amramu: Aaroni ndi Mose. Aaroni ndi zidzukulu zake anapatulidwa kwamuyaya kuti azipereka zinthu zopatulika kwambiri monga nsembe pamaso pa Yehova, komanso kuti azitumikira pamaso pake ndi kumadalitsa anthu mʼdzina lake kwamuyaya. Ana a Mose munthu wa Mulungu anawerengedwa ngati gawo la fuko la Levi. Ana a Mose: Geresomu ndi Eliezara. Zidzukulu za Geresomu: Mtsogoleri anali Subaeli. Zidzukulu za Eliezara: Mtsogoleri anali Rehabiya. Eliezara analibe ana ena aamuna, koma ana a Rehabiya anali ochuluka kwambiri. Ana a Izihari: Mtsogoleri anali Selomiti. Ana a Hebroni: Mtsogoleri anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, Yahazieli anali wachitatu ndipo Yekameamu anali wachinayi. Ana a Uzieli: Mtsogoleri anali Mika ndipo wachiwiri anali Isiya. Banja la Merari Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Ana a Mahili: Eliezara ndi Kisi. Eliezara anamwalira wopanda ana aamuna. Iye anali ndi ana aakazi okhaokha. Abale awo, ana a Kisi, ndiwo amene anawakwatira. Ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yeremoti. Onse analipo atatu. Izi zinali zidzukulu za Levi mwa mabanja awo, atsogoleri a mabanja monga momwe analembedwera mayina awo ndi monga momwenso anawerengedwera, banja lililonse pa lokha. Awa ndi anthu ogwira ntchito oyambira zaka makumi awiri zobadwa kapena kupitirirapo, amene amatumikira mʼNyumba ya Yehova. Popeza Davide anati, “Pakuti Yehova Mulungu wa Israeli, wapereka mpumulo kwa anthu ake ndipo wabwera kudzakhala mu Yerusalemu kwamuyaya, sikofunikiranso kuti Alevi azinyamula tenti kapena zipangizo za chipembedzo.” Potsata malangizo otsiriza a Davide, Alevi anawerengedwa kuyambira amuna a zaka makumi awiri zakubadwa kapena kupitirirapo. Ntchito ya Alevi inali kuthandiza zidzukulu za Aaroni pa ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova monga kuyangʼanira mabwalo, zipinda zamʼmbali, kuyeretsa zinthu zonse zachipembedzo, ndiponso kuchita ntchito zina za mʼnyumba ya Mulungu. Iwo amayangʼanira buledi amene amayikidwa pa tebulo, ufa wa nsembe yachakudya, timitanda ta buledi wopanda yisiti: kuphika ndi kusakaniza, ndiponso miyeso yonse ndi kukula kwake. Iwo amayimiriranso mmawa uliwonse kuthokoza ndi kutamanda Yehova. Amachitanso chomwecho madzulo, ndiponso popereka nsembe zopsereza kwa Yehova pa Sabata ndi pa chikondwerero cha Mwezi Watsopano, ndi pa nthawi yosankhidwa ya Chikondwerero. Iwo amatumikira pamaso pa Yehova nthawi zonse mwa chiwerengero chawo ndi momwe analangizidwira. Ndipo kotero Alevi anachita ntchito yawo ya ku tenti ya msonkhano ya ku Malo Opatulika ndiponso molamulidwa ndi abale awo, zidzukulu za Aaroni, pa ntchito ya mʼNyumba ya Yehova. Magulu a Ansembe Magulu a ana a Aaroni anali awa: Ana a Aaroni anali Nadabu, Abihu, Eliezara ndi Itamara. Koma Nadabu ndi Abihu anamwalira abambo awo asanamwalire, ndipo analibe ana aamuna. Kotero Eliezara ndi Itamara ankatumikira monga ansembe. Mothandizidwa ndi Zadoki chidzukulu cha Eliezara ndi Ahimeleki chidzukulu cha Itamara, Davide anawagawa mʼmagulu molingana ndi ntchito yawo yotumikira. Atsogoleri ambiri anapezeka pakati pa zidzukulu za Eliezara kusiyana ndi zidzukulu za Itamara ndipo anagawidwa moyenera: atsogoleri 16 a mabanja ochokera kwa Eliezara, ndipo atsogoleri asanu ndi atatu a mabanja ochokera kwa zidzukulu za Itamara. Anawagawa mosakondera pochita maere, pakuti iwo anali akuluakulu a ku malo opatulika ndi akuluakulu a Mulungu pakati pa zidzukulu za Eliezara ndi Itamara. Mlembi Semaya mwana wa Netaneli, Mlevi, analemba mayina awo pamaso pa mfumu ndi akuluakulu ake: wansembe Zadoki, Ahimeleki mwana wa Abiatara ndi atsogoleri a mabanja a ansembe ndiponso Alevi, banja limodzi kuchokera kwa Eliezara kenaka limodzi kuchokera kwa Itamara. Maere woyamba anagwera Yehoyaribu, achiwiri anagwera Yedaya, achitatu anagwera Harimu, achinayi anagwera Seorimu, achisanu anagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi anagwera Miyamini, achisanu ndi chiwiri anagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu anagwera Abiya, achisanu ndi chinayi anagwera Yesuwa, a khumi anagwera Sekaniya, a 11 anagwera Eliyasibu, a 12 anagwera Yakimu, a 13 anagwera Hupa, a 14 anagwera Yesebeabu, a 15 anagwera Biliga, a 16 anagwera Imeri, a 17 anagwera Heziri, a 18 anagwera Hapizezi, a 19 anagwera Petahiya, a 20 anagwera Ezekieli, a 21 anagwera Yakini, a 22 anagwera Gamuli, a 23 anagwera Delaya, ndipo a 24 anagwera Maaziya. Umu ndi mmene anasankhidwira kuti azigwira ntchito yotumikira pamene alowa mʼNyumba ya Yehova, motsatira dongosolo limene anapatsidwa ndi kholo lawo Aaroni, monga momwe Yehova Mulungu wa Israeli anamulamulira. Alevi Ena Onse Za zidzukulu zina zonse za Levi: Kuchokera kwa ana a Amramu: Subaeli; kuchokera kwa ana a Subaeli: Yehideya. Kwa Rehabiya, kuchokera kwa ana ake: Mtsogoleri anali Isiya. Kuchokera ku banja la Izihari: Selomoti; kuchokera kwa ana a Selomoti: Yahati. Ana a Hebroni: woyamba anali Yeriya, wachiwiri anali Amariya, wachitatu anali Yahazieli ndipo Yekameamu anali wachinayi. Mwana wa Uzieli: Mika; kuchokera kwa ana a Mika: Samiri. Mʼbale wa Mika: Isiya; kuchokera kwa ana a Isiya: Zekariya. Ana a Merari: Mahili ndi Musi. Mwana wa Yaaziya: Beno. Ana a Merari: Kuchokera kwa Yaaziya: Beno, Sohamu, Zakuri ndi Ibiri. Kuchokera kwa Mahili: Eliezara, amene analibe ana aamuna. Kuchokera kwa Kisi: Mwana wa Kisi: Yerahimeeli. Ndipo ana a Musi: Mahili, Ederi ndi Yerimoti. Awa anali Alevi potsata mabanja a makolo awo. Iwonso anachita maere, monga anachitira abale awo, zidzukulu za Aaroni, pamaso pa mfumu Davide, ndi Zadoki ndi Ahimeleki, atsogoleri a mabanja a ansembe ndi Alevi. Mabanja a mwana wamkulu anachita nawo mofanana ndi a mwana wamngʼono. Anthu Oyimba Nyimbo Davide ndi atsogoleri a asilikali anapatula ena mwa ana a Asafu, Hemani ndi Yedutuni ku utumiki wa uneneri pogwiritsa ntchito apangwe, azeze ndi ziwaya zamalipenga. Tsopano nawu mndandanda wa anthu amene ankagwira ntchito imeneyi: Kuchokera kwa ana a Asafu: Zakuri, Yosefe, Netaniya ndi Asareli. Ana a Asafu amalamulidwa ndi Asafu ndipo amanenera moyangʼaniridwa ndi mfumu. Kwa Yedutuni, kuchokera kwa ana ake: Gedaliya, Zeri, Yesaya, Simei, Hasabiya ndi Matitiya. Onse analipo 9 ndipo amayangʼaniridwa ndi Yedutuni abambo awo, amene amanenera pogwiritsa ntchito apangwe poyamika ndi kutamanda Yehova. Kwa Hemani, kuchokera kwa ana ake: Bukiya, Mataniya, Uzieli, Subaeli ndi Yerimoti; Hananiya, Hanani, Eliata, Gidaliti ndi Romamiti-Ezeri; Yosibakasa, Maloti, Hotiri ndi Mahazioti. Onsewa anali ana a Hemani mlosi wa mfumu. Iye anapatsidwa anawa potsata mawu a Mulungu akuti adzamukweza. Mulungu anapatsa Hemani ana aamuna 14 ndi ana aakazi atatu. Anthu onsewa ankayangʼaniridwa ndi makolo awo pa mayimbidwe a mʼNyumba ya Yehova. Iwowatu ankayimba ndi ziwaya zamalipenga, azeze ndi apangwe potumikira mʼNyumba ya Mulungu. Koma Asafu, Yedutuni ndi Hemani amayangʼaniridwa ndi mfumu. Iwo pamodzi ndi abale awo onse ophunzitsidwa ndi aluso loyimbira Yehova chiwerengero chawo chinali 288. Angʼonoangʼono ndi akulu omwe, mphunzitsi ndi wophunzira yemwe anachita maere pa ntchito zawo. Maere woyamba amene anali a Asafu, anagwera Yosefe,    ana ndi abale ake. 12 Maere achiwiri anagwera Gedaliya,    ndi abale ake ndi ana ake. 12 Maere achitatu anagwera Zakuri,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere achinayi anagwera Iziri,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere achisanu anagwera Netaniya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere achisanu ndi chimodzi anagwera Bukiya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere achisanu ndi chiwiri anagwera Yesarela,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere achisanu ndi chitatu anagwera Yeshaya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere achisanu ndi chinayi anagwera Mataniya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a khumi anagwera Simei,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 11 anagwera Azareli,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 12 anagwera Hasabiya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 13 anagwera Subaeli,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 14 anagwera Matitiya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 15 anagwera Yeremoti,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 16 anagwera Hananiya,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 17 anagwera Yosibakasa,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 18 anagwera Hanani,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 19 anagwera Maloti,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 20 anagwera Eliyata,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 21 anagwera Hotiri,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 22 anagwera Gidaliti,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 23 anagwera Mahazioti,    ana ake ndi abale ake. 12 Maere a 24 anagwera Romamiti-Ezeri,    ana ake ndi abale ake 12.
Alonda a pa Zipata Magulu a alonda a pa zipata: Kuchokera ku banja la Kora: Meselemiya mwana wa Kore, mmodzi mwa ana a Asafu. Meselemiya anali ndi ana awa: woyamba Zekariya, wachiwiri Yediaeli, wachitatu Zebadiya, wachinayi Yatinieli, wachisanu Elamu, wachisanu ndi chimodzi Yehohanani, ndipo wachisanu ndi chiwiri Elihunai. Obedi-Edomu analinso ndi ana awa: woyamba Semaya, wachiwiri Yehozabadi, wachitatu Yowa, wachinayi Sakara, wachisanu Netaneli, wachisanu ndi chimodzi Amieli, wachisanu ndi chiwiri Isakara ndipo wachisanu ndi chitatu Peuletayi. (Pakuti Mulungu anadalitsa Obedi-Edomu). Mwana wake Semaya analinso ndi ana amene anali atsogoleri mʼbanja la abambo awo chifukwa anali anthu amphamvu. Ana a Semaya anali: Otini, Refaeli, Obedi ndi Elizabadi; abale ake, Elihu ndi Semakiya, analinso anthu amphamvu. Onsewa anali adzukulu a Obedi-Edomu. Iwo ndi ana awo ndiponso abale awo anali anthu aluso ndi amphamvu pogwira ntchito. Zidzukulu zonse za Obedi-Edomu zinalipo 62. Meselemiya anali ndi ana ndi abale ake amene anali aluso ndipo onse analipo 18. Hosa Mmerari anali ndi ana awa: woyamba anali Simiri (ngakhale kuti iye sanali woyamba kubadwa, abambo ake anamusankha kuti akhale mtsogoleri), wachiwiri Hilikiya, wachitatu Tebaliya ndipo wachinayi Zekariya. Ana ndi abale onse a Hosa analipo 13. Magulu amenewa a alonda a pa zipata, motsogozedwa ndi atsogoleri awo, anali ndi ntchito yotumikira mʼNyumba ya Yehova, monga momwe amachitira abale awo. Iwo anachita maere mwa mabanja awo aangʼono ndi aakulu omwe kuti apeze mlonda pa chipata chilichonse. Maere a chipata chakummwa anagwera Selemiya. Maere anachitikanso chifukwa cha mwana wake Zekariya, phungu wanzeru ndipo maere a chipata chakumpoto anagwera iye. Maere a chipata chakummwera anagwera Obedi-Edomu, ndipo maere a nyumba yosungiramo katundu anagwera ana ake. Maere a chipata chakumadzulo ndi chipata cha Saleketi ku msewu wa ku mtunda anagwera Supimu ndi Hosa. Mlonda ankayangʼanana ndi mlonda mnzake: Mbali ya kummawa kunkakhala Alevi 6 pa tsiku, kumpoto anayi pa tsiku, kummwera anayi pa tsiku ndipo awiri ankakhala pa nyumba yosungiramo katundu. Ndipo ku bwalo cha kumadzulo, anayi amakhala mu msewu ndi awiri pabwalo penipeni. Awa anali magulu a alonda a pa zipata amene anali zidzukulu za Kora ndi Merari. Asungichuma ndi Akuluakulu Ena Abale awo Alevi, motsogozedwa ndi Ahiya, anali oyangʼanira chuma cha nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Mulungu. Adzukulu a Ladani, mmodzi mwa ana a Geresoni, amene anali atsogoleri a mabanja a Ageresoni, anali awa: Yehieli, ana a Yehieli, Zetamu ndi mʼbale wake Yoweli. Iwo amayangʼanira chuma cha ku Nyumba ya Mulungu wa Yehova. Kuchokera ku banja la Amramu, banja la Aizihara, banja la Ahebroni ndi banja la Auzieli: Subaeli, chidzukulu cha Geresomu, mwana wa Mose, anali mkulu woyangʼanira chuma. Abale ake obadwa mwa Eliezara, anali Rekabiya mwana wake, Yesaya mwana wake, Yoramu mwana wake, Zikiri mwana wake ndi Selomiti mwana wake. Selomiti ndi abale ake amayangʼanira zinthu zonse zoperekedwa kwa Mulungu ndi mfumu Davide, atsogoleri a mabanja amene anali olamulira ankhondo 1,000, olamulira ankhondo 100, ndi olamulira ankhondo ena. Zina zofunkha ku nkhondo anazipereka kuti zikhale zokonzera Nyumba ya Yehova. Ndipo zonse zimene zinaperekedwa ndi Mlosi Samueli, Sauli mwana wa Kisi, Abineri mwana wa Neri ndiponso Yowabu mwana wa Zeruya ndi zinthu zonse zimene zinkaperekedwa zimasungidwa ndi Selomiti ndi abale ake. Kuchokera ku banja la Izihari: Kenaniya ndi ana ake anapatsidwa ntchito kutali ndi Nyumba ya Mulungu ngati akuluakulu ndi oweruza Israeli. Kuchokera ku banja la Ahebroni: Hasabiya ndi abale ake, anthu anzeru 1,700. Iwo ankayangʼanira ntchito zonse za Yehova ndi ntchito yonse ya mfumu cha kumadzulo kwa Yorodani. Pa banja la Ahebroni, Yeriya anali mtsogoleri monga mwa mbiri ya mibado ya mabanja awo. Mʼchaka cha 40 cha ufumu wa Davide, panachitika kafukufuku ndipo ena mwa anthu aluso a banja la Hebroni anapezeka kuti anali ku Yazeri ku Giliyadi. Yeriya anali ndi abale 2,700 amene anali aluso ndiponso atsogoleri a mabanja. Mfumu Davide anawayika iwowa kuti aziyangʼanira fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi theka la fuko la Manase pa zinthu zonse za Mulungu ndi za mfumu. Magulu a Anthu Ankhondo Uwu ndi mndandanda wa Aisraeli, atsogoleri a mabanja, olamulira asilikali 1,000, olamulira asilikali 100 ndi akuluakulu awo, amene ankatumikira mfumu mʼzonse zokhudza magulu a ankhondo, amene amagwira ntchito mwezi ndi mwezi chaka chonse. Gulu lililonse linali ndi anthu 24,000. Amene amalamulira gulu loyamba pa mwezi woyamba anali Yasobeamu mwana wa Zabidieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Iyeyu anali chidzukulu cha Perezi ndipo anali mkulu wa atsogoleri onse a ankhondo mwezi woyamba. Amene amalamulira gulu lachiwiri pa mwezi wachiwiri anali Dodai Mwahohi; Mikiloti ndiye anali mtsogoleri wa gulu lake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Wolamulira ankhondo wachitatu, pa mwezi wachitatu anali Benaya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye anali mtsogoleri ndipo pa gulu lake panali ankhondo 24,000. Uyu ndi Benaya uja amene anali wamphamvu pa gulu la anthu makumi atatu ndipo ndiye amatsogolera anthu makumi atatu aja. Mwana wake Amizabadi ndiye amatsogolera gulu lake. Wachinayi pa mwezi wachinayi anali Asaheli mʼbale wake wa Yowabu; ndipo mwana wake Zebadiya ndiye analowa mʼmalo mwake. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Wachisanu pa mwezi wachisanu anali Samihuti, mdzukulu wa Izira. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Wa 6 pa mwezi wa 6 anali Ira mwana wa Ikesi wa ku Tekowa. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Wa 7 pa mwezi wa 7 anali Helezi Mpeloni wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Wa 8 pa mwezi wa 8 anali Sibekai Mhusati, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000 Wa 9 pa mwezi wa 9 anali Abiezeri wa banja la Anatoti, wa fuko la Benjamini. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Wa khumi pa mwezi wa khumi anali Mahazayi wa ku Netofa, wa mbumba ya Zera. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri wa 11, pa mwezi wa 11 anali Benaya wa ku Piratoni, wa fuko la Efereimu. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Mtsogoleri wa 12, pa mwezi wa 12 anali Helidai Mnetofa, wa banja la Otanieli. Pa gulu lake panali asilikali 24,000. Akuluakulu a Mafuko a Israeli Akuluakulu amene amatsogolera mafuko a Israeli ndi awa: Mtsogoleri wa fuko la Rubeni: Eliezara mwana wa Zikiri; mtsogoleri wa fuko la Simeoni: Sefatiya mwana wa Maaka; mtsogoleri wa fuko la Levi: Hasabiya mwana wa Kemueli, mtsogoleri wa banja la Aaroni: Zadoki; mtsogoleri wa fuko la Yuda: Elihu, mʼbale wake wa Davide; mtsogoleri wa fuko la Isakara: Omuri mwana wa Mikayeli; mtsogoleri wa fuko la Zebuloni: Isimaiya mwana wa Obadiya; mtsogoleri wa fuko la Nafutali: Yerimoti mwana wa Azirieli; mtsogoleri wa fuko la Efereimu: Hoseya mwana wa Azaziya; mtsogoleri wa fuko la theka la Manase: Yoweli mwana wa Pedaya; mtsogoleri wa fuko la theka la Manase limene linali ku Giliyadi: Ido mwana wa Zekariya; mtsogoleri wa fuko la Benjamini: Yaasieli mwana wa Abineri; mtsogoleri wa fuko la Dani: Azareli mwana wa Yerohamu. Awa anali akuluakulu a mafuko a Israeli. Davide sanawerenge amuna amene anali ndi zaka makumi awiri kapena kucheperapo, chifukwa Yehova analonjeza kuti adzachulukitsa Aisraeli ngati nyenyezi zamumlengalenga. Yowabu mwana wa Zeruya anayamba kuwerenga amuna koma sanamalize. Mkwiyo unagwera Aisraeli chifukwa cha zimenezi ndipo chiwerengerochi sanachilowetse mʼbuku la mbiri ya mfumu Davide. Anthu Oyangʼanira Chuma cha Mfumu Azimaveti mwana wa Adieli ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa mfumu. Yonatani mwana wa Uziya ankayangʼanira nyumba zosungiramo katundu wa maboma ozungulira, mizinda, midzi ndi malo olondera. Eziri mwana wa Kelubi ankayangʼanira anthu ogwira ntchito yolima ku munda. Simei wa ku Rama ankayangʼanira minda ya mpesa. Zabidi wa ku Sifamu ankayangʼanira mphesa ndi mosungiramo mwake. Baala-Hanani wa ku Gederi ankayangʼanira mitengo ya olivi ndi ya mikuyu ya ku Sefela. Yowasi ankayangʼanira mafuta a Olivi. Sitirayi wa ku Saroni ankayangʼanira ziweto zimene amaweta ku Saroni. Safati mwana wa Adilayi ankayangʼanira ngʼombe zakuzigwa. Obili Mwismaeli ankayangʼanira ngamira. Yehideya Mmerenoti ankayangʼanira abulu. Yazizi Mhagiri akayangʼanira nkhosa ndi mbuzi. Onsewa anali akuluakulu oyangʼanira chuma cha mfumu Davide. Yonatani, malume wake wa Davide, anali phungu wake ndipo anali munthu wanzeru komanso analinso mlembi. Yehieli mwana wa Hakimoni ankasamalira ana a mfumu. Ahitofele anali phungu wa mfumu. Husai Mwariki anali bwenzi la mfumu. Ahitofele atamwalira mʼmalo mwake munalowa Yehoyada mwana wa Benaya ndi Abiatara. Yowabu anali mtsogoleri wa gulu lankhondo la mfumu. Ndondomeko ya Kamangidwe ka Nyumba ya Mulungu Davide anayitana akuluakulu onse a Israeli kuti asonkhane ku Yerusalemu: akuluakulu a mafuko, olamulira magulu a ntchito ya mfumu, olamulira ankhondo 1,000, ndi olamulira ankhondo 100, ndiponso akuluakulu onse osunga katundu ndi ziweto za mfumu ndi ana ake, pamodzinso ndi akuluakulu a ku nyumba yaufumu, anthu amphamvu ndi asilikali onse olimba mtima. Mfumu Davide inayimirira ndipo inati: “Tamverani abale anga ndi anthu anga. Ine ndinali ndi maganizo omanga nyumba monga malo okhalamo Bokosi la Chipangano la Yehova, malo oyikapo mapazi a Mulungu wathu, ndipo ndinakonza ndondomeko yomangira nyumbayo.” Koma Mulungu anati kwa ine, “Usandimangire nyumba chifukwa ndiwe munthu wankhondo ndipo wakhala ukukhetsa magazi.” “Komabe Yehova Mulungu wa Israeli anasankha ine pakati pa onse a banja langa kukhala mfumu ya Israeli kwamuyaya. Iye anasankha Yuda kukhala mtsogoleri, ndipo pa banja la Yuda anasankha banja langa. Pakati pa ana aamuna a abambo anga, kunamukomera Iye kundikhazika mfumu ya Aisraeli onse. Pa ana anga ambiri onse amene Yehova wandipatsa, Iye wasankha mwana wanga Solomoni kuti akhale pa mpando waufumu wa ufumu wa Yehova kuti alamulire Israeli.” Yehova anati kwa ine, “Solomoni mwana wako ndiye amene adzamanga nyumba yanga ndi mabwalo anga, pakuti Ine ndamusankha kuti akhale mwana wanga ndipo Ine ndidzakhala abambo ake. Ine ndidzakhazikitsa ufumu wake kwamuyaya ngati iye saleka kutsatira malamulo ndi malangizo anga, monga momwe zikuchitikira leromu.” “Tsono lero ine ndikulamula inu pamaso pa Aisraeli onse ndi pa msonkhano wa Yehova, ndipo Mulungu wathu akumva: Mutsatire mosamala malamulo a Yehova Mulungu wathu, kuti dziko labwinoli likhale lanu ndi kuti mudzalipereke kwa zidzukulu zanu kukhala cholowa chawo kwamuyaya.” “Ndipo iwe mwana wanga Solomoni, umvere Mulungu wa abambo ako, umutumikire ndi mtima wodzipereka kwathunthu ndi mtima wako wonse, pakuti Yehova amasanthula mtima wa aliyense, ndipo amadziwa maganizo aliwonse a munthu. Ngati ufunafuna Yehova, Iye adzapezeka; koma ngati umutaya, Iye adzakukana kwamuyaya. Tsopano ganizira bwino, pakuti Yehova wakusankha iwe kuti umange Nyumba ya Mulungu monga malo ake opatulika. Khala wamphamvu ndipo ugwire ntchito.” Kotero Davide anapatsa Solomoni mwana wake mapulani a khonde la Nyumba ya Mulungu, nyumba zake, mosungiramo katundu, zipinda zake zamʼmwamba, zipinda zamʼkati ndi malo a nsembe zopepesera machimo. Iye anapatsa Solomoni mapulani a zonse zimene ankaziganizira za bwalo la Nyumba ya Yehova ndi zipinda zonse zozungulira, zipinda zosungiramo chuma cha Nyumba ya Mulungu ndi zinthu zoperekedwa kwa Yehova. Davide anamulangiza za magulu a ansembe ndi Alevi ndi ntchito yonse yotumikira mʼNyumba ya Yehova, komanso za zinthu zonse zogwirira ntchito potumikira. Iye anakonzeratu za kulemera kwa golide wopangira zida zonse zagolide zogwirira ntchito zosiyanasiyana, ndiponso kulemera kwa siliva wopangira zida zonse zasiliva zogwirira ntchito zosiyanasiyana: kulemera kwa golide wopangira choyikapo nyale chagolide ndi nyale zake; ndiponso kulemera kwa siliva wa choyikapo nyale chilichonse ndi nyale zake, molingana ndi kagwiritsidwe ka choyikapo nyale chilichonse; kulemera kwa golide wa tebulo iliyonse yoyikapo buledi wopatulika; kulemera kwa siliva wopangira matebulo asiliva; muyeso wa golide woyengeka bwino wopangira mafoloko, mbale ndi zotungira; muyeso wa golide wa beseni lililonse la siliva; ndiponso muyeso wa golide wabwino wopangira guwa la zofukiza. Davide anamupatsanso ndondomeko ya mapangidwe a galeta, akerubi agolide atatambasula mapiko awo kuphimba Bokosi la Chipangano la Yehova. Davide anati, “Zonsezi ndalemba kuchokera kwa Yehova, ndipo Iye wachita kuti ndimvetsetse zonse za mapulaniwa.” Davide anatinso kwa mwana wake Solomoni, “Khala wamphamvu ndi wolimba mtima ndipo uchite ntchitoyi. Usachite mantha kapena kutaya mtima pakuti Yehova Mulungu wanga ali nawe. Iye sadzakukhumudwitsa kapena kukusiya mpaka ntchito yonse ya Nyumba ya Mulungu itatha. Magulu a ansembe ndi Alevi ndi okonzeka kugwira ntchito ya Nyumba ya Mulungu, ndipo munthu waluso aliyense wodzipereka adzakuthandiza pa ntchito yonse. Akuluakulu ndi anthu onse adzamvera chilichonse chomwe udzalamula.” Zopereka Zomangira Nyumba ya Mulungu Kenaka, mfumu Davide inati kwa gulu lonse: “Mwana wanga Solomoni amene Mulungu wamusankha ndi wamngʼono ndipo sadziwa zambiri. Ntchitoyi ndi yayikulu chifukwa nyumba yaufumuyi si ya munthu, koma ndi ya Yehova Mulungu. Ine ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu zinthu zanga zonse, golide wopangira zinthu zagolide, siliva wopangira zinthu zasiliva ndi zitsulo zopangira zinthu zazitsulo, mkuwa wopangira zinthu zamkuwa ndi matabwa opangira zinthu zamatabwa komanso miyala yokongola ya onikisi yokongoletsera, miyala ya maonekedwe osiyanasiyana, ndi miyala yonse yosalala ndi miyala ya marabulo, zonsezi ndapereka zochuluka. Kupatulapo izi, ine modzipereka ku Nyumba ya Mulungu wanga, tsopano ndikupereka chuma changachanga cha golide ndi siliva ku Nyumba ya Mulungu wanga, kuwonjezera pa zimene ndapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu woyerayu: Matani 100 agolide (golide wa ku Ofiri) ndi matani 240 a siliva woyengeka bwino wokutira makoma a nyumba, zinthu zagolide ndi zinthu zasiliva, ndiponso zinthu zonse zimene anthu aluso adzagwiritse ntchito. Tsopano ndani amene akufuna kudzipatulira yekha kwa Yehova lero?” Tsono atsogoleri a mabanja, akuluakulu a mafuko a Israeli, olamulira asilikali 1,000, ndi olamulira asilikali 100, ndiponso akuluakulu onse amene amayangʼanira ntchito ya mfumu anapereka mwaufulu. Iwo anapereka ku ntchito ya Nyumba ya Mulungu matani 170 a golide, matani 340 a siliva, matani 620 a mkuwa ndi matani 3,400 a chitsulo. Aliyense amene anali ndi miyala yokongola anayipereka ku nyumba yosungiramo chuma cha Nyumba ya Yehova ndipo amene ankayangʼanira anali Yehieli Mgeresoni. Anthu anakondwa chifukwa cha kupereka mwaufulu kwa atsogoleri awo, pakuti anapereka kwa Yehova mwaufulu ndiponso ndi mtima wonse. Nayenso mfumu Davide anakondwera kwambiri. Pemphero la Davide Davide anatamanda Yehova pamaso pa gulu lonse, ponena kuti, “Mutamandidwe Inu Yehova Mulungu wa kholo lathu Israeli kuchokera muyaya mpaka muyaya. Wanu, Inu Yehova ndi ukulu ndi mphamvu, ulemerero ndiponso ufumu ndi kukongola. Pakuti zinthu zonse zakumwamba ndi pa dziko lapansi ndi zanu. Wanu, Inu Yehova ndi ufumu; Inu ndinu wokwezeka ndipo ndinu mtsogoleri wa zonse. Chuma ndi ulemu zimachokera kwa Inu; Inu ndinu wolamulira zinthu zonse. Mʼdzanja lanu muli nyonga ndi mphamvu, kukweza ndi kupereka nyonga kwa onse. Tsopano Mulungu wathu, ife tikukuthokozani ndi kutamanda dzina lanu laulemerero. “Koma ine ndine yani, ndipo anthu anga ndani, kuti tikupatsani mowolowamanja motere? Zinthu zonse zimachokera kwa Inu, ndipo ife takupatsani zomwe zimachokera mʼdzanja lanu. Ife ndife anthu osadziwika ndiponso alendo pamaso panu, monga analili makolo athu. Masiku anthu pa dziko lapansi ali ngati chithunzithunzi, wopanda chiyembekezo. Inu Yehova Mulungu wathu, zinthu zonse zimene tapereka kumangira Nyumba yanu zachokera mʼdzanja lanu ndipo zonsezi ndi zanu. Mulungu wanga, ine ndikudziwa kuti mumayesa mtima ndipo mumakondwera ndi anthu angwiro. Zinthu zonsezi ndapereka mwaufulu ndi cholinga chabwino. Ndipo tsopano ndaona ndi chimwemwe momwe anthu anu amene ali pano akuperekera mwaufulu kwa Inu. Inu Yehova Mulungu wa makolo athu Abrahamu, Isake ndi Israeli, mukhazikitse chofuna ichi mʼmitima ya anthu anu kwamuyaya, ndipo mukhazikitse mtima wokhulupirika kwa Inu. Ndipo mumupatse mwana wanga Solomoni mtima wodzipereka kwathunthu kwa Inu kuti asunge malamulo anu, zofuna ndi malangizo anu. Achite chilichonse pomanga nyumba yaufumu imene ine ndayipezera zofunika zonse.” Kenaka mfumu Davide inati kwa gulu lonse, “Tamandani Yehova Mulungu wanu.” Kotero onse anatamanda Yehova, Mulungu wa makolo awo ndipo anawerama pansi ndi kugona chafufumimba pamaso pa Yehova ndi mfumu. Solomoni Avomerezedwa Monga Mfumu Mmawa mwake anthu anapereka nsembe zosiyanasiyana ndi nsembe zopsereza kwa Yehova; ngʼombe zamphongo 1,000, nkhosa zamphongo 1,000 ndi ana ankhosa 1,000, pamodzi ndi nsembe yachakumwa ndi nsembe zina zambiri zoperekera Aisraeli onse. Tsiku limeneli, iwo anadya ndi kumwa mosangalala pamaso pa Yehova ndipo anavomereza Solomoni mwana wa Davide kukhala mfumu yawo kachiwiri. Anamudzoza pamaso pa Yehova kukhala wolamulira wawo ndipo Zadoki anadzozedwa kukhala wansembe. Ndipo Solomoni ankakhala pa mpando waufumu wa Yehova monga mfumu mʼmalo mwa Davide abambo ake. Iye analemera ndipo Aisraeli onse ankamumvera. Akuluakulu onse a ankhondo ndi anthu amphamvu, pamodzinso ndi ana onse aamuna a mfumu Davide, analonjeza kumvera mfumu Solomoni. Yehova anamukweza kwambiri Solomoni pamaso pa Aisraeli onse ndi kumupatsa ulemerero waufumu umene sunapatsidwepo kwa mfumu ina iliyonse ya Israeli. Imfa ya Davide Davide mwana wa Yese anali mfumu ya Aisraeli onse. Iye analamulira Israeli kwa zaka makumi anayi; zaka zisanu ndi ziwiri ali ku Hebroni ndi zaka 33 ali ku Yerusalemu. Iye anamwalira atakalamba kwambiri, atakhala ndi moyo wautali, chuma ndi ulemu. Solomoni mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. Tsono zonse zimene mfumu Davide anachita, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mneneri Samueli, mʼbuku la mneneri Natani ndi mʼbuku la mneneri Gadi, pamodzi ndi tsatanetsatane wa mbiri ya ulamuliro wake ndi mphamvu zake, ndi zonse zomwe zinamuzungulira iye ndi Israeli ndiponso mafumu a mayiko ena onse.